Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Proverbs 1:1-31:31
  • Miyambo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miyambo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Miyambo

Miyambo

1 Miyambi+ ya Solomo+ mwana wa Davide,+ mfumu ya Isiraeli,+ 2 yothandiza munthu kupeza nzeru+ ndi malangizo,*+ kuti amvetse mawu ozama,+ 3 kuti alandire malangizo+ amene amathandiza munthu kuzindikira,+ kuchita zolondola,+ zachilungamo+ ndi zowongoka.+ 4 Yothandiza kuti munthu wosadziwa akhale wochenjera,+kuti wachinyamata akhale wodziwa zinthu+ ndiponso kuti azitha kuganiza bwino.+

5 Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka,+ ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake,+ 6 kuti azitha kumvetsa mwambi ndi mawu ozunguza mutu,+ mawu a anthu anzeru+ ndi mikuluwiko yawo.+

7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu.+ Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.*+

8 Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako,+ ndipo usasiye malamulo a mayi ako,+ 9 pakuti zimenezi zili ngati nkhata ya maluwa yokongola pamutu pako,+ ndi mkanda wokongola m’khosi mwako.+

10 Mwana wanga, ochimwa akayesa kukunyengerera usavomere.+ 11 Akamanena kuti: “Tiye tipitire limodzi. Tiye tikabisalire anthu kuti tikakhetse magazi.+ Tiye tikabisalire anthu osalakwa. Tikachite zimenezo popanda chifukwa chilichonse.+ 12 Tiye tikawameze amoyo+ ngati mmene amachitira Manda,*+ tikawameze athunthu ngati amene akupita kudzenje.+ 13 Tiye tikapeze zinthu zamtengo wapatali zosiyanasiyana.+ Tiye tidzaze nyumba zathu ndi zofunkha.+ 14 Tiye tichitire limodzi maere. Tonsefe tikhale ndi chikwama chimodzi chokha.”+ 15 Mwana wanga, usayende nawo limodzi panjira.+ Letsa phazi lako kuti lisayende panjira yawo.+ 16 Chifukwa mapazi awo amathamangira zoipa,+ ndipo iwo amafulumira kukakhetsa magazi.+ 17 N’zopanda phindu kuyala ukonde pamaso pa chilichonse chokhala ndi mapiko.+ 18 Chotero anthu ochimwa amabisala kuti akhetse magazi a anthu ena.+ Amabisalira miyoyo ya anthu ena.+ 19 Umu ndi mmene zimakhalira njira za aliyense wopeza phindu mwachinyengo.+ Phindulo limachotsa moyo wa eni akewo.+

20 Nzeru yeniyeni+ imangokhalira kufuula mumsewu.+ Imangokhalira kutulutsa mawu ake m’mabwalo a mzinda.+ 21 Iyo imafuula kumapeto kwa misewu yaphokoso.+ Pazipata zolowera mumzinda, imanena mawu ake kuti:+

22 “Anthu osadziwa inu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa mpaka liti?+ Inu onyoza, mukufuna kukhalabe onyoza mpaka liti?+ Ndipo opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+ 23 Mverani kudzudzula kwanga ndipo mubwerere.+ Mukatero ndidzachititsa kuti mzimu wanga usefukire kwa inu+ ndipo ndidzakudziwitsani mawu anga.+ 24 Popeza ndaitana koma inu mukupitiriza kukana,+ ndatambasula dzanja langa koma palibe amene akumvetsera,+ 25 mukungonyalanyaza malangizo anga onse,+ ndipo simunamvere kudzudzula kwanga,+ 26 ineyo ndidzakusekani tsoka likadzakugwerani.+ Ndidzakunyozani zimene mumaopa zikadzabwera,+ 27 zimene mumaopa zikadzabwera ngati mvula yamkuntho, tsoka likadzakufikirani ngati mphepo yamkuntho,+ ndiponso masautso ndi nthawi zovuta zikadzakugwerani.+ 28 Pa nthawi imeneyo azidzangondiitana koma sindidzayankha.+ Adzakhalira kundifunafuna koma sadzandipeza,+ 29 chifukwa chakuti anadana ndi kudziwa zinthu+ ndipo sanasankhe kuopa Yehova.+ 30 Sanamvere malangizo anga.+ Sanalemekeze kudzudzula kwanga konse.+ 31 Chotero adzadya zipatso za njira yawo,+ ndipo adzakhuta malangizo awo.+ 32 Pakuti kupanduka+ kwa osadziwa n’kumene kudzawaphe+ ndipo mphwayi za opusa n’zimene zidzawawononge.+ 33 Koma munthu wondimvera adzakhala mwabata+ ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”+

2 Mwana wanga, ukamvera mawu anga+ ndi kusunga malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali,+ 2 ukamvetsera nzeru ndi khutu lako,+ ukaika mtima wako pa kuzindikira,+ 3 komanso ukaitana kumvetsa zinthu+ ndi kufuulira kuzindikira,+ 4 ukamazifunafuna ngati siliva,+ ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+ 5 udzamvetsa tanthauzo la kuopa+ Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu.+ 6 Pakuti Yehova amapereka nzeru.+ Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.+ 7 Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.+ Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, iye amakhala chishango+ 8 mwa kuyang’anitsitsa njira zachiweruzo,+ ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+ 9 Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.+

10 Nzeru zikalowa mumtima mwako,+ ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa m’moyo wako,+ 11 kuganiza bwino kudzakuyang’anira,+ ndipo kuzindikira kudzakuteteza,+ 12 kuti kukupulumutse kunjira yoipa,+ ndiponso kwa munthu wonena zinthu zopotoka,+ 13 komanso kwa anthu amene amasiya njira zowongoka kuti ayende m’njira za mdima.+ 14 Kudzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala kuchita zoipa,+ amene amakondwera ndi zinthu zoipa ndi zopotoka,+ 15 amene njira zawo ndi zokhota ndiponso amene ali achinyengo m’zochita zawo zonse.+ 16 Kudzakupulumutsa kwa mkazi wachilendo, mkazi wochokera kwina+ wolankhula mwaukathyali,+ 17 amene wasiya mnzake wapamtima wa pachitsikana chake+ ndiponso amene waiwala pangano limene anapangana ndi Mulungu wake.+ 18 Pakuti nyumba yake imatsikira kumanda ndipo njira zake zimatsikira kwa akufa.+ 19 Onse ogona naye sadzabwerera ndipo iwo sadzapezanso njira za amoyo.+

20 Cholinga cha zonsezi n’chakuti uziyenda m’njira ya anthu abwino+ ndi kuti uzisunga njira za anthu olungama.+ 21 Pakuti owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi,+ ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.+ 22 Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi+ ndipo achinyengo adzazulidwamo.+

3 Mwana wanga, usaiwale lamulo langa,+ ndipo mtima wako usunge malamulo anga.+ 2 Ukatero, udzakhala ndi masiku ochuluka, moyo wazaka zambiri,+ ndi mtendere.+ 3 Usasiye kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+ Uzimange m’khosi mwako+ ndiponso uzilembe pamtima pako.+ 4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.+ 5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,+ ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.+ 6 Uzim’kumbukira m’njira zako zonse,+ ndipo iye adzawongola njira zako.+

7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.+ 8 Zimenezi zidzachiritsa+ mchombo wako ndi kutsitsimutsa mafupa ako.+

9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+ 10 Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza+ ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.+

11 Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+ ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+ 12 chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda,+ monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.+

13 Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru,+ ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira,+ 14 chifukwa kupeza nzeru monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide.+ 15 N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. 16 Masiku ochuluka ali m’dzanja lake lamanja.+ M’dzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.+ 17 Njira zake n’zobweretsa chisangalalo ndipo misewu yake yonse ndi yamtendere.+ 18 Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo+ kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa+ adzatchedwa odala.+

19 Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+ Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+ 20 Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuya,+ ndipo kumwamba kwa mitambo kumagwetsa mvula yamawawa.+ 21 Mwana wanga, zimenezi zisachoke pamaso pako.+ Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino,+ 22 ndipo zidzatanthauza moyo kwa iwe+ komanso zidzakhala chokongoletsa m’khosi mwako.+ 23 Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,+ ndipo ngakhale phazi lako silidzapunthwa ndi chilichonse.+ 24 Nthawi iliyonse ukagona sudzaopa chilichonse.+ Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+ 25 Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+ kapena mphepo yamkuntho yowomba oipa, chifukwa ikubwera.+ 26 Pakuti Yehova ndiye amene uzidzamudalira,+ ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+

27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo,+ pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.+ 28 Usanene kwa mnzako kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndidzakupatsa,” pamene uli ndi chinachake choti ungam’patse.+ 29 Usakonze zochitira mnzako choipa,+ pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.+ 30 Usakangane ndi munthu popanda chifukwa,+ ngati sanakuchitire choipa.+

31 Usasirire munthu wachiwawa,+ kapena kusankha njira zake.+ 32 Pakuti munthu wochita zachiphamaso+ Yehova amanyansidwa naye,+ koma amakonda anthu owongoka mtima.+ 33 Temberero la Yehova lili panyumba ya munthu woipa,+ koma malo okhala anthu olungama, iye amawadalitsa.+ 34 Onyoza,+ iye amawanyoza,+ koma ofatsa amawakomera mtima.+ 35 Anzeru adzapeza ulemu,+ koma opusa amatama zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+

4 Ananu, mverani malangizo* a bambo anu.+ Mvetserani kuti mupeze luso lomvetsa zinthu.+ 2 Pakuti ndithu ndidzakupatsani malangizo abwino.+ Musasiye lamulo langa.+ 3 Pakuti ine ndinali mwana wabwino kwa bambo anga.+ Ndinali wokondedwa kwambiri ndiponso mmodzi yekhayo pamaso pa mayi anga.+ 4 Bambo anga anali kundilangiza+ kuti: “Mtima wako+ ugwire mwamphamvu mawu anga.+ Sunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+ 5 Upeze nzeru,+ upezenso luso lomvetsa zinthu.+ Usaiwale ndipo usapatuke pa mawu a m’kamwa mwanga.+ 6 Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakusunga. Uzikonde ndipo zidzakuteteza. 7 Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.+ Peza nzeru, ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+ 8 Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+ Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+ 9 Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.+ Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.”+

10 Tamvera mwana wanga, ndipo utsatire mawu anga.+ Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka.+ 11 Ndidzakutsogolera m’njira ya nzeru.+ Ndidzakuchititsa kuyenda m’njira zowongoka.+ 12 Ukamayenda, sudzayenda mopanikizika+ ndipo ngati ukuthamanga sudzapunthwa.+ 13 Gwira malangizo,+ usawataye.+ Uwasunge bwino chifukwa iwo ndiwo moyo wako.+

14 Usalowe panjira ya oipa,+ ndipo usalunjike kunjira ya ochita zoipa.+ 15 Uipewe,+ uilambalale.+ Upatukepo, n’kupitirira.+ 16 Pakuti iwo sagona kufikira atachita zoipa.+ Tulo sitiwabwerera mpaka atakhumudwitsa wina.+ 17 Pakuti amadya mkate wa zoipa+ ndipo amamwa vinyo wachiwawa.+ 18 Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.+ 19 Njira ya oipa ili ngati mdima.+ Iwo sadziwa chimene chimawapunthwitsa.+

20 Mwana wanga, mvetsera mawu anga.+ Tchera khutu lako ku zonena zanga.+ 21 Zisachoke pamaso pako.+ Uzisunge mkati mwa mtima wako.+ 22 Pakuti izo ndi moyo kwa amene amazipeza+ ndiponso ndi thanzi labwino kwa thupi lawo lonse.+ 23 Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa,+ pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.+ 24 Chotsa mawu opotoka pakamwa pako,+ ndipo milomo yachinyengo uiike kutali ndi iwe.+ 25 Maso ako aziyang’ana patsogolo.+ Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.+ 26 Salaza njira ya phazi lako,+ ndipo njira zako zonse zikhazikike.+ 27 Usakhotere kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Chotsa phazi lako pa zoipa.+

5 Mwana wanga, mvetsera nzeru zanga.+ Tchera makutu ako ku zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kuzindikira,+ 2 kuti uteteze kuganiza bwino,+ ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+

3 Pakuti milomo ya mkazi wachilendo imakha uchi ngati chisa cha njuchi+ ndipo m’kamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+ 4 Koma zotsatirapo zochokera kwa iye n’zowawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+ N’zakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+ 5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.+ Miyendo yake imalowera ku Manda.+ 6 Iye saganizira njira ya moyo.+ Amangoyendayenda panjira zake osadziwa kumene akupita.+ 7 Tsopano ananu ndimvereni,+ ndipo musapatuke pa mawu otuluka m’kamwa mwanga.+ 8 Njira yako ikhale kutali ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+ 9 kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+ kapena kupereka zaka zako ku zinthu zankhanza.+ 10 Ndiponso kuti alendo asakhute mphamvu zako,+ kuti zinthu zimene unazipeza movutikira* zisakhale m’nyumba ya mlendo,+ 11 komanso kuti usadzabuule m’tsogolo+ mnofu ndi thupi lako zikadzafika ku mapeto kwake.+ 12 Pa nthawiyo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine,+ ndipo mtima wanga sunkavomereza kudzudzula.+ 13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,+ ndipo sindinatchere khutu kwa aphunzitsi anga.+ 14 N’chifukwa chake mosayembekezeka ndinagwera m’zinthu zoipa zamtundu uliwonse,+ ndipo ndinachita manyazi pamaso pa mpingo wonse.”+

15 Imwa madzi ochokera m’chitsime chako, komanso madzi oyenderera kuchokera pakati pa chitsime chako.+ 16 Kodi akasupe ako amwazike panja,+ ndipo mitsinje yako yamadzi imwazike m’mabwalo a mumzinda? 17 Zimenezi zikhale zako zokha osatinso za alendo amene ali nawe.+ 18 Kasupe wa madzi ako akhale wodalitsidwa,+ ndipo usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.+ 19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yokondedwa ndiponso ngati mbuzi yokongola ya m’mapiri.+ Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse.+ Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.+ 20 Chotero pali chifukwa chanji choti usangalalire ndi mkazi wachilendo mwana wanga, kapena choti ukumbatirire chifuwa cha mkazi wina?+ 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ 22 Woipa adzagwidwa ndi zolakwa zake zomwe,+ ndipo adzamangidwa m’zingwe za tchimo lake lomwe.+ 23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,+ ndiponso chifukwa chakuti amasocheretsedwa ndi zopusa zake zochuluka.+

6 Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+ ngati wagwirana chanza ndi mlendo pochita mgwirizano,+ 2 ngati wakodwa ndi mawu a m’kamwa mwako,+ ngati wagwidwa ndi mawu a m’kamwa mwako, 3 uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse, pakuti wagwa m’manja mwa mnzako:+ Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+ 4 Maso ako asapeze tulo, ndipo maso ako owala asagone.+ 5 Dzipulumutse ngati insa m’manja mwa wosaka, ndiponso ngati mbalame m’manja mwa wosaka mbalame.+

6 Pita kwa nyerere+ waulesi iwe,+ ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru. 7 Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira, 8 imakonza chakudya chake m’chilimwe.+ Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola. 9 Kodi ugonabe mpaka liti, waulesiwe?+ Udzuka nthawi yanji kutulo tako?+ 10 Ukapitiriza kugona pang’ono, ukapitiriza katulo pang’ono, ukapitiriza kupinda manja pang’ono pogona,+ 11 umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,+ ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

12 Munthu wopanda pake,+ wochita zopweteka anzake, amayenda ndi mawu opotoka.+ 13 Amatsinzinira ena ndi diso lake,+ amapanga zizindikiro ndi phazi lake, ndiponso amapanga zizindikiro ndi zala zake.+ 14 Mumtima mwake muli zopotoka.+ Nthawi zonse amakhala akukonza zoipa.+ Amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15 N’chifukwa chake tsoka lake lidzabwere mwadzidzidzi.+ Adzathyoledwa modzidzimutsa, ndipo sadzachira.+

16 Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.+ Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo:+ 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+ 18 mtima wokonzera ena ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa,+ 19 mboni yachinyengo yonena mabodza,+ ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.+

20 Mwana wanga, sunga lamulo la bambo ako,+ ndipo usasiye malangizo a mayi ako.+ 21 Ulimange pamtima pako nthawi zonse+ ndipo ulimange m’khosi mwako.+ 22 Lidzakutsogolera ukamayenda,+ lidzakulondera ukamagona,+ ndipo ukadzuka, lidzakusamalira. 23 Pakuti lamulolo ndilo nyale,+ ndipo malangizo ndiwo kuwala,+ komanso kudzudzula* kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo,+ 24 kuti kukuteteze kwa mkazi woipa,+ komanso ku lilime losalala la mkazi wachilendo.+ 25 Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+ Asakukope ndi maso ake owala,+ 26 pakuti munthu amafika potsala ndi mkate wozungulira umodzi wokha chifukwa cha hule,+ koma mkazi wamwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.+ 27 Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28 Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29 N’chimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.+ Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+ 30 Anthu sanyoza munthu wakuba, akaba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31 Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7. Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake.+ 32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru mumtima mwake.+ Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.+ 33 Adzapeza tsoka ndi manyazi,+ ndipo kunyozeka kwake sikudzafufutika.+ 34 Pakuti nsanje ya mwamuna imautsa mkwiyo wake,+ ndipo sadzamva chisoni pa tsiku lobwezera.+ 35 Iye sadzavomera dipo* lamtundu uliwonse, ndipo sadzalola ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

7 Mwana wanga, sunga mawu anga+ ndipo usunge malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali.+ 2 Sunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo+ ndipo usunge lamulo langa ngati mwana+ wako wa diso. 3 Uwamange kuzala zako,+ ndipo uwalembe pamtima pako.+ 4 Uza nzeru+ kuti: “Ndiwe mlongo wanga,” ndipo kumvetsa zinthu ukutche “M’bale wanga wamkazi,” 5 kuti utetezedwe kwa mkazi wachilendo,+ ndiponso kwa mkazi wochokera kwina amene amalankhula mawu okopa.+ 6 Pakuti ndinayang’ana pansi kuchokera pawindo* la nyumba yanga,+ 7 kuti ndione anthu osadziwa zinthu.+ Ndinkafuna kuona mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake amene anali pakati pa ana aamuna.+ 8 Mnyamatayo anali kuyenda mumsewu pafupi ndi mphambano yopita kunyumba ya mkazi wachilendo. Iye anali kuyenda panjira yopita kunyumba ya mkaziyo,+ 9 pa nthawi ya madzulo kuli kachisisira,+ kutatsala pang’ono kuda. 10 Ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye atavala zovala zosonyeza kuti ndi hule.+ Mkaziyo anali wamtima wachinyengo, 11 wolongolola ndiponso wamakani.*+ Mapazi ake sakhala m’nyumba mwake.+ 12 Amapezeka panja, m’mabwalo a mzinda,+ ndiponso amakhala akudikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+ 13 Iye wagwira mnyamatayo n’kumupsompsona.+ Kenako, m’maso muli gwaa! akuyamba kumuuza kuti:

14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.+ Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza.+ 15 N’chifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe, kudzafunafuna nkhope yako kuti ndikupeze. 16 Ndayala zofunda pabedi panga. Ndayalaponso nsalu za ku Iguputo zamitundu yosiyanasiyana.+ 17 Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+ 18 Bwera tisonyezane chikondi mpaka chitikwane. Tichite zimenezi mpaka m’mawa. Tisangalatsane pouzana mawu achikondi.+ 19 Pakuti mwamuna wanga sali kunyumba. Iye wayenda ulendo wopita kutali.+ 20 Wanyamula chikwama cha ndalama m’manja mwake. Iye adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzakhale wathunthu.”

21 Mkaziyo wamusocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+ Wamunyengerera ndi milomo yake yotulutsa mawu okopa.+ 22 Mwadzidzidzi mnyamatayo wayamba kulondola mkaziyo+ ngati ng’ombe yamphongo yopita kokaphedwa, ndiponso ngati kuti wamangidwa m’matangadza kuti alandire chilango* cha munthu wopusa. 23 Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi* chake,+ ngati mbalame yothamangira kumsampha,+ ndipo iye sakudziwa kuti zikukhudza moyo wake.+

24 Tsopano ananu ndimvereni, ndipo mverani mawu otuluka m’kamwa mwanga.+ 25 Mtima wako usapatukire kunjira zake. Iweyo usayendeyende m’njira zake.+ 26 Pakuti mkaziyo waphetsa anthu ambiri,+ ndipo onse amene aphedwa ndi iye ndi ochuluka.+ 27 Nyumba yake ndiyo njira ya ku Manda.+ Imatsikira kuzipinda za imfa.+

8 Nzerutu ikungokhalira kufuula,+ ndipo kuzindikira kukungokhalira kutulutsa mawu.+ 2 Imaima pamwamba pa zitunda,+ m’mbali mwa njira ndi pamphambano za misewu. 3 Imafuula mokweza+ pambali pa zipata, pakhomo la mzinda ndi polowera kuzipata,+ kuti:

4 “Ndikufuulira anthu inu, ndipo mawu anga akupita kwa ana a anthu.+ 5 Inu osadziwa zinthu, phunzirani kukhala ochenjera.+ Anthu opusa inu, pezani mtima womvetsa zinthu.+ 6 Mvetserani chifukwa ndikulankhula zinthu zofunika kwambiri.+ Ndikutsegula pakamwa panga kuti ndinene zowongoka.+ 7 Pakuti pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,+ ndipo milomo yanga imaipidwa ndi zoipa.+ 8 Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.+ Pa mawu anga palibe zokhota kapena zopotoka.+ 9 Mawu anga onse ndi osavuta kumva kwa wozindikira, ndipo ndi owongoka kwa anthu odziwa zinthu.+ 10 Landirani malangizo* anga osati siliva, ndiponso kudziwa zinthu m’malo mwa golide wabwino kwambiri.+ 11 Pakuti nzeru n’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zosangalatsa zonse sizingafanane nazo.+

12 “Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera,+ ndimadziwa zinthu, ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+ 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ 14 Ine ndili ndi malangizo+ ndi nzeru zopindulitsa.+ Ndimamvetsa zinthu,+ ndiponso ndili ndi mphamvu.+ 15 Chifukwa cha ine, mafumu amalamulira. Nazonso nduna zapamwamba zimakhazikitsa malamulo olungama.+ 16 Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,+ ndipo anthu onse olemekezeka amaweruza mwachilungamo.+ 17 Amene amandikonda, inenso ndimawakonda.+ Amene amandifunafuna ndi amene amandipeza.+ 18 Chuma ndi ulemerero zili ndi ine.+ Ndilinso ndi cholowa chamtengo wapatali ndi chilungamo.+ 19 Zipatso zanga n’zabwino kuposa golide. N’zoposa ngakhale golide woyengedwa bwino. Zokolola zanga n’zoposa siliva wabwino kwambiri.+ 20 Ndimayenda m’njira yachilungamo,+ komanso pakati pamisewu yachilungamo,+ 21 kuti ndichititse amene amandikonda kulandira zinthu zamtengo wapatali,+ ndipo ndimadzazitsa nkhokwe zawo.+

22 “Yehova anandipanga monga chiyambi cha njira yake.+ Ine ndiye ntchito yoyambirira pa ntchito zake zimene anakwaniritsa kalekale kwambiri.+ 23 Ndinakhazikitsidwa kuyambira nthawi yosadziwika,+ kuyambira pa chiyambi, kuyambira nthawi zakale kuposa dziko lapansi.+ 24 Ndinabadwa ndi ululu wa pobereka kulibe madzi akuya,+ kulibe akasupe odzaza madzi. 25 Mapiri akuluakulu asanakhazikitsidwe,+ mapiri ang’onoang’ono asanakhalepo, ine ndinabadwa ndi ululu wa pobereka, 26 iye asanapange dziko lapansi,+ zigwa zopanda kanthu, ndi zibuma zoyamba za dothi lachonde la padziko lapansi.+ 27 Pamene anali kukonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+ Pamene anakhazikitsa lamulo lakuti pamwamba pa madzi akuya pazioneka pozungulira,+ 28 pamene analimbitsa mitambo yakumwamba,+ pamene anachititsa kuti akasupe a madzi akuya akhale olimba,+ 29 pamene anaikira nyanja lamulo lake lakuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+ pamene anakhazikitsa maziko a dziko lapansi,+ 30 ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+ Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambiri ndi ine.+ Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+ 31 Ndinali kusangalala ndi nthaka ya dziko lake lapansi,+ ndipo zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.+

32 “Tsopano ananu, ndimvereni. Ndithu, odala ndiwo amene amasunga njira zanga.+ 33 Mverani malangizo kuti mukhale anzeru,+ ndipo musawanyalanyaze.+ 34 Wodala ndi munthu amene amandimvetsera mwa kukhala maso pamakomo anga tsiku ndi tsiku, mwa kuyang’anitsitsa pamafelemu a makomo anga.+ 35 Pakuti wondipeza ine, ndithu adzapezanso moyo+ ndipo Yehova adzasangalala naye,+ 36 koma wolephera kundipeza akupweteka moyo wake.+ Onse odana ndi ine ndiye kuti amakonda imfa.”+

9 Nzeru yeniyeni+ yamanga nyumba yake.+ Yasema zipilala zake 7. 2 Yapha nyama yake ndipo yasakaniza vinyo wake. Kuwonjezera apo, yayala patebulo pake.+ 3 Yatuma antchito ake aakazi kuti apite pamwamba pa zitunda za m’mudzi akaiitanire anthu, kuti: 4 “Aliyense wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense wopanda nzeru mumtima mwake,+ nzeru* ikumuuza kuti: 5 “Bwerani mudzadye chakudya changa ndiponso mudzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.+ 6 Alekeni anthu osadziwa zinthu kuti mupitirize kukhala ndi moyo,+ ndipo yendani mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.”+

7 Amene amalangiza wonyoza amadzichotsera yekha ulemu,+ ndipo amene amadzudzula woipa amadzibweretsera chilema.+ 8 Usadzudzule wonyoza kuti angadane nawe.+ Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+ 9 Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+ Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.

10 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+ 11 Pakuti ine ndidzachititsa kuti masiku ako akhale ambiri+ ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.+ 12 Ngati wakhala wanzeru, nzeruzo zidzapindulitsa iweyo.+ Ngati uli wonyoza, iweyo ndiye udzavutike.+

13 Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+ Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.+ 14 Wakhala pampando pakhomo la nyumba yake, pachitunda cha m’mudzimo,+ 15 kuti aziitana anthu odutsa amene akuyenda panjira zawo atalunjika kutsogolo. Iye akuwauza kuti:+ 16 “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense amene ali wopanda nzeru mumtima mwake,+ mkaziyo wamuuza kuti: 17 “Madzi akuba amatsekemera,*+ ndipo mkate wakudya mwakabisira umakoma.”+ 18 Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa, ndiponso kuti amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.+

10 Miyambi ya Solomo.+

Mwana wanzeru amakondweretsa bambo ake,+ koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.+ 2 Chuma cha anthu oipa chidzakhala chopanda phindu,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+ 3 Yehova sadzachititsa munthu wolungama kukhala ndi njala,+ koma zolakalaka za anthu oipa adzazikankhira kumbali.+

4 Wogwira ntchito ndi dzanja laulesi adzakhala wosauka,+ koma dzanja la munthu wakhama ndi limene limalemeretsa.+

5 Mwana wozindikira amatuta m’chilimwe. Mwana wochititsa manyazi amakhala ali m’tulo tofa nato pa nthawi yokolola.+

6 Madalitso amapita pamutu pa wolungama,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+ 7 Anthu akamakumbukira zabwino zimene munthu wolungama anali kuchita, amam’dalitsa,+ koma dzina la anthu oipa lidzawola.+

8 Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malamulo,+ koma wamilomo yopusa amaponderezedwa.+

9 Woyenda ndi mtima wosagawanika adzayenda popanda chomuopseza,+ koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.+

10 Wotsinzinira ena ndi diso lake adzamvetsa ena ululu,+ ndipo wamilomo yopusa adzaponderezedwa.+ 11 Pakamwa pa wolungama m’pamene pamachokera moyo,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+

12 Chidani n’chimene chimayambitsa mikangano,+ koma chikondi chimaphimba machimo onse.+

13 Pamilomo ya munthu womvetsa zinthu pamapezeka nzeru,+ koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+

14 Anzeru ndiwo amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+ koma pakamwa pa wopusa patsala pang’ono kuwonongeka.+

15 Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma zili ngati mudzi wake wolimba.+ Chiwonongeko cha onyozeka ndicho umphawi wawo.+

16 Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.+ Zokolola za woipa zimabweretsa tchimo.+

17 Amene wagwira malangizo* mwamphamvu ndiye njira ya kumoyo,+ koma wosiya chidzudzulo amasocheretsa anthu.+

18 Pamene pali munthu wobisa chidani pamakhala milomo yonyenga,+ ndipo wobweretsa uthenga woipa ndi wopusa.+

19 Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+

20 Lilime la wolungama ndilo siliva wabwino kwambiri.+ Mtima wa woipa ndi wopanda phindu.+

21 Milomo ya wolungama imaweta anthu ambiri,+ koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru mumtima.+

22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+

23 Kwa wopusa, kusonyeza khalidwe lotayirira kuli ngati masewera,+ koma nzeru zimakhala ndi munthu wozindikira.+

24 Chinthu choopsa kwa woipa n’chimene chidzamubwerere,+ koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+ 25 Woipa amatha ngati momwe zimakhalira pakawomba mphepo yamkuntho,+ koma wolungama ndiye maziko mpaka kalekale.*+

26 Monga mmene amakhalira vinyo wowawasa m’mano ndiponso utsi m’maso, ndi mmenenso amakhalira munthu waulesi kwa amene am’tuma.+

27 Kuopa Yehova kudzawonjezera masiku,+ koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+

28 Zoyembekezera za olungama zimasangalatsa,+ koma chiyembekezo cha oipa chidzawonongeka.+

29 Njira ya Yehova ndiyo malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzawonongedwa.+

30 Wolungama sadzagwedezedwa mpaka kalekale,+ koma anthu oipa sadzapitiriza kukhala padziko lapansi.+

31 Pakamwa pa wolungama pamabala zipatso za nzeru,+ koma lilime lonena zopotoka lidzadulidwa.+

32 Milomo ya wolungama imavomerezedwa ndi Mulungu,*+ koma pakamwa pa anthu oipa m’popotoka.+

11 Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova,+ koma mwala woyezera, wolemera mokwanira, umam’sangalatsa.

2 Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+

3 Mtima wosagawanika wa anthu owongoka ndi umene umawatsogolera,+ koma kupotoza zinthu kwa anthu ochita zachinyengo kudzawawononga.+

4 Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+

5 Kulungama kwa munthu wopanda cholakwa n’kumene kudzawongole njira yake,+ koma woipa adzagwera m’zoipa zakezo.+ 6 Kulungama kwa anthu owongoka mtima n’kumene kudzawapulumutse,+ koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+

7 Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimawonongeka,+ ndipo zimene anali kuyembekezera kuchokera ku mphamvu zake sizichitika.+

8 Wolungama ndi amene amapulumutsidwa ku zowawa,+ ndipo woipa amalowa m’malo mwake.+

9 Wopanduka amawononga mnzake ndi pakamwa pake,+ koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+

10 Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+

11 Mudzi umakwezedwa chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+ koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+

12 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amanyoza mnzake,+ koma munthu wozindikira bwino ndi amene amakhala chete.+

13 Amene amayendayenda n’kumanenera ena zoipa+ amaulula zinsinsi za anzake,+ koma wokhulupirika* amabisa nkhani.+

14 Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.+ Koma pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+

15 Munthu amene walonjeza kuti adzapereka ngongole ya mlendo iye akadzalephera kubweza,+ zinthu sizidzamuyendera bwino. Koma wodana ndi kugwirana chanza pochita mgwirizano sakhala ndi nkhawa.

16 Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+ Koma anthu ochitira nkhanza anzawo amapeza chuma.

17 Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake,+ koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.+

18 Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+ koma wofesa chilungamo amapeza malipiro enieni.+

19 Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+ koma munthu wofunafuna zoipa adzafa.+

20 Anthu a mtima wopotoka amam’nyansa Yehova,+ koma anthu opanda cholakwa m’njira yawo amam’sangalatsa.+

21 Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake, munthu woipa sadzapewa chilango,+ koma ana a anthu olungama adzapulumuka ndithu.+

22 Monga momwe chimakhalira chipini* chagolide pamphuno ya nkhumba, ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola koma wosaganiza bwino.+

23 Zolakalaka za anthu olungama, ndithu n’zabwino.+ Chiyembekezo cha oipa chimabweretsa mkwiyo woopsa.+

24 Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+

25 Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto,+ ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.+

26 Wokana kugulitsa mbewu zake kwa anthu, anthuwo adzam’temberera. Koma wolola kuzigulitsa adzalandira madalitso.+

27 Wofunafuna kuchitira ena zabwino, amafunafuna kuvomerezedwa ndi Mulungu.*+ Koma wofunafuna kuchita zoipa, zoipazo zidzam’bwerera.+

28 Wodalira chuma chake adzagwa,+ koma anthu olungama adzasangalala ngati masamba a zomera.+

29 Aliyense wochititsa nyumba yake kunyanyalidwa+ adzagwira mphepo,+ ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wa mtima wanzeru.

30 Zipatso za munthu wolungama ndizo mtengo wa moyo,+ ndipo munthu wopulumutsa miyoyo ndi wanzeru.+

31 Wolungamatu adzalandira mphoto yake padziko lapansi.+ Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+

12 Wokonda malangizo* amakondanso kudziwa zinthu,+ koma wodana ndi chidzudzulo ndi wopanda nzeru.+

2 Munthu wabwino Yehova amakondwera naye,+ koma munthu wamaganizo oipa iye amamutcha woipa.+

3 Palibe munthu amene angakhazikike chifukwa chochita zoipa,+ koma muzu wa anthu olungama sudzagwedezedwa.+

4 Mkazi wabwino ndi chisoti cha ulemu kwa mwamuna wake,*+ koma mkazi wochita zinthu zochititsa manyazi ali ngati chowoletsa mafupa a mwamunayo.+

5 Maganizo a anthu olungama ndiwo chilungamo.+ Utsogoleri wa anthu oipa ndi wachinyengo.+

6 Mawu a anthu oipa amadikirira kukhetsa magazi,+ koma pakamwa pa anthu owongoka mtima m’pamene padzawapulumutse.+

7 Anthu oipa amagonjetsedwa n’kusakhalaponso,+ koma nyumba ya anthu olungama idzakhalapobe.+

8 Munthu adzatamandidwa chifukwa cha pakamwa pake panzeru,+ koma wa mtima wopotoka adzanyozedwa.+

9 Kuli bwino kukhala munthu wamba koma n’kukhala ndi wantchito, kusiyana n’kukhala wodzikuza koma wopanda chakudya.+

10 Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake,+ koma chisamaliro cha anthu oipa n’chankhanza.+

11 Wolima nthaka yake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+ koma wofunafuna zinthu zopanda pake ndi wopanda nzeru mumtima mwake.+

12 Woipa amalakalaka nyama yokodwa mumsampha wa anthu oipa,+ koma muzu wa anthu olungama umabala zipatso.+

13 Munthu woipa amakodwa ndi kuchimwa kwa milomo yake,+ koma wolungama amachoka m’masautso.+

14 Munthu amakhutitsidwa ndi zabwino kuchokera ku zipatso za pakamwa pake,+ ndipo zochita za manja a munthu, zidzabwerera kwa iye.+

15 Njira ya munthu wopusa imakhala yolondola m’maso mwake,+ koma womvera malangizo ndi wanzeru.+

16 Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa,+ koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.+

17 Wotulutsa mawu okhulupirika amanena zolungama,+ koma mboni yonama imanena zachinyengo.+

18 Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga,+ koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+

19 Mlomo wa choonadi+ ndi umene udzakhazikike kwamuyaya,+ koma lilime lachinyengo lidzangokhalapo kwa kanthawi.+

20 Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,+ koma olimbikitsa mtendere amasangalala.+

21 Palibe chopweteka chimene chidzagwere wolungama,+ koma anthu oipa ndi amene tsoka lizidzangowagwera.+

22 Milomo yonama imam’nyansa Yehova,+ koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amam’sangalatsa.+

23 Munthu wochenjera amabisa zimene akudziwa,+ koma mtima wa anthu opusa umalengeza zopusa.+

24 Dzanja la anthu akhama n’limene lidzalamulire,+ koma dzanja laulesi lidzagwira ntchito yaukapolo.+

25 Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa,+ koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.+

26 Wolungama amayendera msipu wake, koma njira ya anthu oipa imawachititsa kuyenda uku ndi uku.+

27 Ulesi sungavumbulutse nyama zimene munthu akufuna kusaka,+ koma munthu wakhama ndiye chuma chamtengo wapatali cha munthu.

28 M’njira yachilungamo muli moyo,+ ndipo ulendo wa m’njira imeneyi suthera ku imfa.+

13 Mwana amakhala wanzeru ngati akulandira malangizo* kuchokera kwa bambo ake.+ Koma amene sanamve chidzudzulo amakhala wonyoza.+

2 Munthu adzadya zipatso zabwino kuchokera pa zipatso za pakamwa pake.+ Koma moyo wa anthu ochita zachinyengo umalakalaka kuchita chiwawa.+

3 Amene amayang’anira pakamwa pake amasunga moyo wake.+ Amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+

4 Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho moyo wake ulibe chilichonse.+ Koma anthu akhama adzanenepa.+

5 Wolungama amadana ndi lilime lonama,+ koma anthu oipa amachita zinthu zochititsa manyazi ndipo amadzibweretsera manyazi.+

6 Chilungamo chimateteza munthu amene sachita zopweteka ena,+ koma wochimwa amawonongedwa ndi zoipa.+

7 Pali munthu amene amadzionetsera kuti ndi wolemera koma alibe kalikonse.+ Ndiponso pali munthu amene amaoneka ngati wosauka koma ali ndi zinthu zambiri zamtengo wapatali.

8 Moyo wa munthu udzawomboledwa ndi chuma chake,+ koma munthu wosauka sadzudzulidwa.+

9 Kuwala kwa anthu olungama kudzawachititsa kusangalala.+ Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+

10 Chifukwa cha kudzikuza, munthu amangoyambitsa mavuto,+ koma anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.+

11 Zinthu zamtengo wapatali zimene zimapezedwa m’njira yachinyengo zimacheperachepera,+ koma wozisonkhanitsa ndi dzanja lake ndi amene amazichulukitsa.+

12 Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.+ Koma chomwe unali kufuna chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+

13 Wokana kusunga mawu,+ wangongole adzamulanda chikole. Koma munthu amene amaopa lamulo ndiye adzalandire mphoto.+

14 Lamulo la munthu wanzeru ndilo kasupe wa moyo,+ chifukwa limapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.+

15 Munthu wozindikira bwino, anthu amam’komera mtima.+ Koma njira ya anthu ochita zachinyengo imakhala yodzaza ndi zopweteka ndiponso mavuto.+

16 Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira,+ koma wopusa amafalitsa uchitsiru.+

17 Mthenga woipa amayambitsa mavuto,+ koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+

18 Munthu wonyalanyaza malangizo amasauka ndipo amadzichotsera ulemu.+ Koma amene amamvera chidzudzulo ndi amene amalemekezedwa.+

19 Zimene umakhumba zikapezeka, moyo umasangalala.+ Koma opusa, kusiya zoipa kumawanyansa.+

20 Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+ koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+

21 Tsoka limatsatira ochimwa,+ koma olungama ndi amene amalandira mphoto zabwino.+

22 Munthu wabwino adzasiyira cholowa zidzukulu zake, ndipo chuma cha wochimwa chimasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+

23 Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,+ koma pali munthu amene wasesedwa chifukwa chosowa chilungamo.+

24 Munthu wosakwapula mwana wake ndiye kuti akumuda,+ koma womukonda ndi amene amamuyang’anira kuti amulangize.+

25 Wolungama amadya n’kukhuta,+ koma mimba za anthu oipa zidzakhala zopanda kanthu.+

14 Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+ koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.+

2 Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova,+ koma munthu amene amayenda m’njira zokhotakhota amanyoza Mulungu.+

3 Chikwapu cha kudzikuza chili m’kamwa mwa wopusa,+ koma anthu anzeru milomo yawo imawatsogolera.+

4 Ngati palibe ng’ombe, chodyeramo chimakhala choyera. Koma zokolola zimachuluka chifukwa cha mphamvu za ng’ombe yamphongo.

5 Mboni yokhulupirika ndi imene sinama,+ koma mboni yonyenga imanena bodza lokhalokha.+

6 Munthu wonyoza amafunafuna nzeru ndipo sazipeza. Koma kudziwa zinthu kumakhala kosavuta kwa munthu womvetsa zinthu.+

7 Choka pamaso pa munthu wopusa,+ chifukwa supeza nzeru m’mawu otuluka pakamwa pake.+

8 Nzeru za munthu wochenjera ndizo kuzindikira njira imene akuyendamo,+ koma kuganiza mopusa kwa zitsiru ndi chinyengo.+

9 Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,+ koma pakati pa anthu owongoka mtima pali mgwirizano.+

10 Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu,+ ndipo mlendo sangalowerere pamene mtimawo ukusangalala.

11 Nyumba za anthu oipa zidzawonongedwa,+ koma mahema a anthu owongoka mtima adzalemera.+

12 Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+

13 Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kukhala ukupweteka.+ Ndipo kusangalala kumathera m’chisoni.+

14 Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakhutira ndi zotsatira za njira zake,+ koma munthu wabwino adzakhutira ndi zotsatira za zochita zake.+

15 Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse,+ koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.+

16 Munthu wanzeru amachita mantha ndipo amapatuka pa choipa,+ koma wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.+

17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+ koma munthu wotha kuganiza bwino amadedwa.+

18 Anthu osadziwa zinthu, ndithu adzakhala opusa,+ koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chovala cha kumutu.+

19 Anthu oipa adzagwadira abwino,+ ndipo oipa adzagwada pazipata za munthu wolungama.

20 Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake,+ koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+

21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+

22 Anthu okonza chiwembu amasochera,+ koma anthu okonzekera kuchita zabwino amapeza kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+

23 Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa,+ koma kungolankhula mawu chabe kumasaukitsa.

24 Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo. Zochita za anthu opusa zimawonjezera kupusa kwawo.+

25 Mboni yoona imapulumutsa anthu,+ koma mboni yonama imangonena bodza.+

26 Munthu woopa Yehova amakhulupirira Mulungu pa chilichonse,+ ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+

27 Kuopa Yehova ndiko chitsime cha moyo,+ chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.+

28 Kuchuluka kwa anthu kumakongoletsa mfumu,+ koma kuchepa kwa anthu kumawonongetsa nduna.+

29 Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri,+ koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.+

30 Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu,+ koma nsanje imawoletsa mafupa.+

31 Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+

32 Woipa adzakankhidwa chifukwa cha kuipa kwake,+ koma wolungama adzapeza malo othawirako chifukwa cha mtima wake wosagawanika.+

33 Mumtima mwa munthu womvetsa zinthu mumakhala nzeru,+ ndipo zimadziwika pakati pa anthu opusa.

34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+ koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu.+

35 Mfumu imasangalala ndi wantchito wochita zinthu mozindikira,+ koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+

15 Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+

2 Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+ koma pakamwa pa zitsiru pamasefukira mawu opusa.+

3 Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+

4 Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo,+ koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.+

5 Aliyense wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+ koma munthu aliyense womvera chidzudzulo ndi wochenjera.+

6 M’nyumba ya munthu wolungama muli katundu wambiri,+ koma katundu wa munthu woipa amabweretsa tsoka.+

7 Milomo ya anzeru imafalitsa zimene ikudziwa,+ koma mtima wa anthu opusa suchita zimenezo.+

8 Nsembe ya anthu oipa imam’nyansa Yehova,+ koma pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa.+

9 Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+ koma iye amakonda munthu wochita chilungamo.+

10 Munthu wosiya njira yabwino amadana ndi malangizo.+ Aliyense wodana ndi chidzudzulo adzafa.+

11 Manda ndiponso malo a chiwonongeko+ zili pamaso pa Yehova.+ Ndiye kuli bwanji mitima ya ana a anthu?+

12 Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akum’dzudzula.+ Iye sadzapita kwa anthu anzeru.+

13 Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala,+ koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.+

14 Mtima womvetsa ndi umene umafunafuna kudziwa zinthu,+ koma pakamwa pa anthu opusa m’pamene pamafunafuna kulankhula zopusa.+

15 Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa,+ koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.+

16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+ kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri koma uli ndi nkhawa.+

17 Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+ kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.+

18 Munthu wopsa mtima amayambitsa mkangano,+ koma munthu wosakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+

19 Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+ koma njira ya anthu owongoka mtima imakhala yosalazidwa bwino.+

20 Mwana wanzeru ndi amene amakondweretsa bambo ake,+ koma wopusa amanyoza mayi ake.+

21 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amakondwera ndi uchitsiru,+ koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+

22 Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima,+ koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.+

23 Munthu amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake,+ ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+

24 Njira ya kumoyo ndi yowongoka kwa munthu wochita zanzeru,+ kuti asatsikire pansi ku Manda.+

25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+

26 Ziwembu za munthu woipa ndi zonyansa kwa Yehova,+ koma mawu osangalatsa ndi oyera pamaso pake.+

27 Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa tsoka panyumba pake,+ koma wodana ndi ziphuphu ndi amene adzakhalebe ndi moyo.+

28 Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamasefukira zoipa.+

29 Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa,+ koma amamva pemphero la anthu olungama.+

30 Maso+ owala amapangitsa mtima kusangalala.+ Uthenga+ wabwino umanenepetsa mafupa.+

31 Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo+ chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.+

32 Aliyense wokana malangizo+ amakana moyo wake, koma munthu womvetsera chidzudzulo amakhala ndi mtima wanzeru.+

33 Kuopa Yehova ndi kumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+ ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+

16 Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake,+ koma kwa Yehova n’kumene kumachokera yankho la palilime lake.+

2 Njira zonse za munthu zimaoneka zoyera m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza zolinga zake.+

3 Pereka ntchito zako kwa Yehova,+ ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.+

4 Yehova anapanga chilichonse n’cholinga,+ ndipo ngakhale woipa anamusungira tsiku loipa.+

5 Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.+ Ngakhale anthu atagwirana manja, munthu sangapewe chilango.+

6 Cholakwa chimaphimbika ndi kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi,+ ndipo chifukwa choopa Yehova munthu amapatuka pa choipa.+

7 Yehova akasangalala ndi njira za munthu,+ amachititsa ngakhale adani a munthuyo kukhala naye pa mtendere.+

8 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa mwachilungamo+ kuposa kukhala ndi zinthu zambiri koma mopanda chilungamo.+

9 Munthu angaganize za njira zake mumtima mwake,+ koma Yehova ndiye amawongolera mayendedwe ake.+

10 Chigamulo chochokera kwa Mulungu chizikhala palilime la mfumu poweruza milandu.+ Pakamwa pake pazikhala pokhulupirika.+

11 Muyezo wachilungamo ndiponso masikelo ndi za Yehova.+ Miyala yonse ya m’thumba loyezera kulemera kwa zinthu ndiyo ntchito zake.+

12 Kuchita zinthu zoipa kumanyansa mafumu,+ chifukwa mpando wachifumu umakhazikika ndi chilungamo.+

13 Milomo yolungama imasangalatsa mfumu yaikulu,+ ndipo mfumuyo imakonda munthu wolankhula zinthu zowongoka.+

14 Mkwiyo wa mfumu umatanthauza amithenga a imfa,+ koma munthu wanzeru ndi amene amauziziritsa.+

15 Nkhope ya mfumu ikawala, zimatanthauza moyo.+ Ndipo mafuno ake abwino ali ngati mtambo wa mvula yomalizira.+

16 Kupeza nzeru n’kwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+ Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+

17 Kupewa zoipa ndiko njira ya anthu owongoka mtima.+ Munthu amene amateteza njira yake, amasunga moyo wake.+

18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+

19 Kuli bwino kukhala wodzichepetsa limodzi ndi anthu ofatsa,+ kusiyana n’kugawana katundu wolanda ndi anthu odzikuza.+

20 Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino,+ ndipo wodala ndi munthu amene amakhulupirira Yehova.+

21 Munthu wanzeru mumtima mwake adzatchedwa wozindikira,+ ndipo munthu wolankhula zabwino amakopa ena ndi mawu a pakamwa pake.+

22 Kuzindikira kumakhala ngati chitsime cha moyo kwa ozindikirawo,+ ndipo malangizo* a anthu opusa ndi uchitsiru.+

23 Mtima wa munthu wanzeru umamuchititsa kuti asonyeze kuzindikira ndi pakamwa pake,+ ndipo umachititsa milomo yake kutulutsa mawu okopa.+

24 Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.+ Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+

25 Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+

26 Munthu wakhama amadzigwirira yekha ntchito+ chifukwa chakuti pakamwa pake pamamukakamiza kwambiri.+

27 Munthu wopanda pake amafukula zinthu zoipa,+ ndipo pakamwa pake pamakhala mawu okhala ngati makala amoto.+

28 Kazitape amangokhalira kuyambitsa mikangano,+ ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.+

29 Munthu wachiwawa amakopa mnzake,+ ndipo amam’chititsa kuti ayende m’njira yoipa.+ 30 Iye amatsinzinira ndi maso ake pokonza ziwembu.+ Amalumirira mano, ndipo amakwanitsadi kuchita chiwembu.

31 Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero+ zikapezeka m’njira yachilungamo.+

32 Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu,+ ndipo munthu wolamulira mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.+

33 Maere amaponyedwa pamwendo,+ koma zonse zimene maerewo amasonyeza zimachokera kwa Yehova.+

17 Kukhala ndi mkate wouma pali bata,+ kuli bwino kuposa nyumba yodzaza ndi nyama yansembe pali mkangano.+

2 Wantchito wochita zinthu mozindikira, adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi,+ ndipo adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.+

3 Siliva amamuyengera m’mbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera m’ng’anjo,+ koma Yehova ndiye amene amayesa mitima.+

4 Wochita zoipa amamvetsera mlomo wolankhula zopweteka ena.+ Wonama amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+

5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+

6 Chisoti chaulemu cha anthu okalamba ndicho zidzukulu zawo,+ ndipo ana amalemekezeka ndi bambo awo.+

7 Munthu aliyense wopusa, mlomo wowongoka sumuyenera.+ Ndiye kuli bwanji mlomo wachinyengo kwa munthu wolemekezeka?+

8 Mphatso ndiyo mwala wamtengo wapatali m’maso mwa mwiniwake wolemekezeka.+ Kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera bwino.+

9 Wophimba machimo akufunafuna chikondi,+ ndipo amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+

10 Kudzudzula kumam’fika pamtima munthu womvetsa zinthu,+ kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+

11 Woipa amangofunafuna kupanduka,+ ndipo munthu amene watumidwa kuti akamulange sam’chitira chifundo.+

12 Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,+ kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chochita zopusa.+

13 Aliyense wobwezera zoipa pa zabwino,+ zoipa sizidzachoka panyumba pake.+

14 Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.+ Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+

15 Aliyense wonena kuti munthu woipa ndi wolungama+ ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi woipa,+ onsewa ndi onyansa kwa Yehova.+

16 N’chifukwa chiyani munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,+ chonsecho alibe zolinga zabwino?*+

17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+

18 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amagwirana chanza ndi munthu wina,+ ndipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+

19 Aliyense wokonda machimo akukonda kulimbana.+ Aliyense wotalikitsa khomo lake akufunafuna kuwonongedwa.+

20 Wa mtima wopotoka sadzapeza zabwino,+ ndipo wa lilime lokhota adzagwera m’tsoka.+

21 Bambo wa mwana wopusa amamva chisoni,+ ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+

22 Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa,+ koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.+

23 Woipa amatenga chiphuphu mobisa,+ kuti akhotetse njira za chiweruzo.+

24 Nzeru zimakhala pamaso pa munthu womvetsa zinthu,+ koma maso a munthu wopusa ali kumalekezero a dziko lapansi.+

25 Mwana wopusa amakhumudwitsa bambo ake,+ ndipo amamvetsa chisoni mayi ake amene anam’bereka.+

26 Komanso, kulipiritsa munthu wolungama si bwino.+ Kumenya anthu olemekezeka n’kosayenera.+

27 Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu,+ ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.+

28 Ngakhale munthu wopusa akakhala chete amaoneka ngati wanzeru,+ ndipo wotseka pakamwa pake amaoneka ngati womvetsa zinthu.

18 Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda.+ Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.+

2 Aliyense wopusa sakondwera ndi kuzindikira zinthu,+ mpaka zimene zili mumtima mwake zitaululika.+

3 Mnyozo umabwera limodzi ndi munthu woipa,+ ndipo chitonzo chimabwera limodzi ndi manyazi.+

4 Mawu a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya.+ Chitsime cha nzeru chili ngati mtsinje wosefukira.+

5 Kukondera munthu woipa si bwino.+ Komanso si bwino kukankhira pambali munthu wolungama poweruza.+

6 Milomo ya munthu wopusa imalowa mu mkangano,+ ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+

7 Pakamwa pa munthu wopusa m’pamene pamamuwononga,+ ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.+

8 Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga,+ zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+

9 Komanso waulesi pa ntchito yake+ ndiye m’bale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+

10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.+

11 Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba,+ ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.+

12 Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+

13 Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa,+ ndipo amachita manyazi.+

14 Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda,+ koma mtima wosweka ndani angaupirire?+

15 Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu,+ ndipo khutu la anzeru limafunafuna kudziwa zinthu.+

16 Mphatso ya munthu imam’tsegulira khomo lalikulu,+ ndipo imakam’fikitsa ngakhale pamaso pa anthu olemekezeka.+

17 Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola,+ koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.+

18 Maere amathetsa mikangano,+ ndipo amalekanitsa ngakhale anthu amphamvu.+

19 M’bale amene walakwiridwa amaposa mzinda wolimba,+ ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekera pachipata cha nsanja yokhalamo.+

20 Mimba ya munthu imakhuta zipatso za pakamwa pake.+ Iye amakhuta ngakhale zokolola za milomo yake.+

21 Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime,+ ndipo wolikonda adzadya zipatso zake.+

22 Kodi munthu wapeza mkazi wabwino?+ Ndiye kuti wapeza chinthu chabwino,+ ndipo Yehova amakondwera naye.+

23 Munthu wosauka amalankhula mochonderera,+ koma munthu wolemera amayankha mwamphamvu.+

24 Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana,+ koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.+

19 Wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika ali bwino kuposa munthu wa milomo yopotoka,+ komanso munthu wopusa.+

2 Ndiponso, si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu,+ ndipo woyenda mofulumira ndi mapazi ake akuchimwa.+

3 Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake,+ choncho mtima wake umakwiyira Yehova.+

4 Chuma chimachulukitsa mabwenzi,+ koma munthu wonyozeka amalekanitsidwa ngakhale kwa bwenzi lake.+

5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+ ndipo wolankhula mabodza sadzapulumuka.+

6 Anthu amene amakhazika pansi mtima wa munthu wolemekezeka ndi ambiri,+ ndipo aliyense amakhala bwenzi la munthu wopereka mphatso.+

7 Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+ komanso anzake amatalikirana naye kwambiri.+ Iye amafuna kuwachonderera, koma iwo amamuthawa.+

8 Munthu amene wapeza mtima wanzeru+ akukonda moyo wake. Wopitiriza kusonyeza kuzindikira amapeza zabwino.+

9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+ ndipo wolankhula mabodza adzawonongedwa.+

10 Aliyense wopusa sayenera moyo wawofuwofu.+ Ndiye kuli bwanji kuti wantchito alamulire akalonga!+

11 Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake,+ ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.+

12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+ koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.+

13 Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+ ndipo mkazi wolongolola ali ngati denga* lodontha limene limathawitsa munthu.+

14 Cholowa chochokera kwa makolo ndicho nyumba ndi chuma,+ koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+

15 Ulesi umachititsa tulo tofa nato,+ ndipo munthu waulesi amakhala ndi njala.+

16 Wosunga lamulo akusunga moyo wake.+ Wosasamala za njira zake adzaphedwa.+

17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

18 Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+ ndipo usalakelake imfa yake.+

19 Wamkwiyo waukulu ayenera kulipitsidwa,+ chifukwa ukam’pulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+

20 Mvera uphungu+ ndipo utsatire malangizo* kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.+

21 Mumtima mwa munthu mumakhala zolinga zambiri,+ koma zolinga za Yehova n’zimene zidzakwaniritsidwe.+

22 Chinthu chosiririka mwa munthu wochokera kufumbi ndicho kukoma mtima kwake kosatha,+ ndipo munthu wosauka ali bwino kuposa munthu wonama.+

23 Kuopa Yehova kumapezetsa moyo.+ Munthu amagona mosatekeseka+ ndipo zoipa sizim’gwera.+

24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera,+ koma n’kulephera kulibweretsa pakamwa.+

25 Menya wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere.+ Ndipo womvetsa zinthu uyenera kum’dzudzula kuti adziwe zinthu zowonjezereka.+

26 Wochitira zoipa bambo ake ndiponso wothamangitsa mayi ake,+ ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+

27 Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo, ndiye kuti wapatuka pa mawu okudziwitsa zinthu.+

28 Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+ ndipo pakamwa pa anthu oipa pamameza zinthu zopweteka ena.+

29 Zilango anazikhazikitsira anthu onyoza,+ ndipo zikwapu anazisungira msana wa anthu opusa.+

20 Vinyo ndi wonyoza.+ Chakumwa choledzeretsa chimasokosera+ ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.+

2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+ Aliyense woputa mkwiyo wake akuchimwira moyo wake womwe.+

3 Kuleka kukangana kumabweretsa ulemerero kwa munthu,+ koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+

4 Chifukwa cha kuzizira, waulesi salima.+ Iye azidzapemphapempha nthawi yokolola koma sadzapatsidwa kanthu.+

5 Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,+ koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.+

6 Pakati pa anthu ambiri, aliyense amanena za kukoma mtima kwake kosatha,+ koma munthu wokhulupirika ndani angam’peze?+

7 Munthu wolungama amayenda ndi mtima wosagawanika,+ ndipo ana ake amakhala odala.+

8 Mfumu imakhala pampando wachiweruzo+ n’kubalalitsa zoipa zonse ndi maso ake.+

9 Ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga,+ ndadziyeretsa ku tchimo langa”?+

10 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+

11 Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.+

12 Khutu lakumva ndiponso diso loona, zonsezi anazipanga ndi Yehova.+

13 Usamakonde tulo kuti ungasauke.+ Tsegula maso ako kuti ukhale ndi zakudya zambiri.+

14 Wogula amati, “Chinthu ichi n’choipa. N’choipa ichi!” Akatero amachoka.+ Kenako amakadzitama.+

15 Pali golide komanso miyala yamtengo wapatali ya korali yambirimbiri, koma milomo yodziwa zinthu ndiyo ziwiya zamtengo wapatali.+

16 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo,+ umulande chovala chake. Ndiponso wochita zoipa ndi mkazi wachilendo umulande chikole.+

17 Munthu amasangalala ndi chakudya chimene wachipeza mwachinyengo,+ koma pambuyo pake, m’kamwa mwake mumadzaza miyala.+

18 Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana,+ ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+

19 Woyenda uku ndi uku n’kumanena zoipa za anthu ena amaulula zinsinsi,+ ndipo usamagwirizane ndi munthu wotengeka ndi milomo yake.+

20 Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+

21 Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba,+ tsogolo lake silidzadalitsidwa.+

22 Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+ Khulupirira Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+

23 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndi yonyansa kwa Yehova,+ ndipo sikelo yachinyengo si yabwino.+

24 Mayendedwe a mwamuna wamphamvu amachokera kwa Yehova,+ koma kodi munthu wochokera kufumbi angazindikire bwanji njira yake?+

25 Umakhala msampha munthu wochokera kufumbi akathamangira kufuula kuti, “N’zoyera!”+ koma pambuyo polonjeza+ n’kumafuna kuganiziranso bwino.+

26 Mfumu yanzeru imabalalitsa anthu oipa,+ ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira.+

27 Mpweya+ wa munthu wochokera kufumbi ndiwo nyale ya Yehova. Imafufuza mosamala mkatikati monse mwa mimba.+

28 Kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi zimateteza mfumu,+ ndipo chifukwa cha kukoma mtima kosatha kumeneko mfumu imakhazikitsa mpando wake wachifumu.+

29 Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo,+ ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.+

30 Zilonda zobwera chifukwa chomenyedwa zimachotsa zoipa,+ ndipo zikwapu zimafika mpaka mkatikati mwa mimba.+

21 Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova.+ Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.+

2 Njira iliyonse ya munthu imaoneka yowongoka m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza mitima.+

3 Kuchita zinthu zoyenera ndi zachilungamo kumamusangalatsa kwambiri Yehova, kuposa kupereka nsembe.+

4 Maso odzikweza ndi mtima wodzikuza+ ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi tchimo.+

5 Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira,+ koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.+

6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira.+ Anthu ochita zinthu mwa njira imeneyi akufunafuna imfa.+

7 Kulanda zinthu za ena kumene anthu oipa amachita n’kumene kudzawawononge,+ chifukwa akana kuchita chilungamo.+

8 Njira ya mlendo imakhala yokhota,+ koma munthu woyera amachita zowongoka.+

9 Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba,+ kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+

10 Moyo wa munthu woipa umalakalaka zoipa,+ ndipo iye akaona mnzake samumvera chisoni.+

11 Mwa kulipiritsa munthu wonyoza, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru.+ Munthu wanzeru akapatsidwa malangizo, amadziwa zinthu.+

12 Mulungu wolungama amayang’ana nyumba ya munthu woipa,+ ndipo anthu oipa amawagwetsa kuti akumane ndi tsoka.+

13 Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,+ nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+

14 Mphatso yoperekedwa mobisa imathetsa mkwiyo,+ ndipo chiphuphu chopereka mobisa chimathetsa+ ukali waukulu.

15 Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzakumana ndi zoipa.+

16 Munthu wochoka pa njira yochita zinthu mozindikira,+ adzapumula mumpingo wa anthu akufa.+

17 Wokonda zosangalatsa adzakhala munthu wosauka.+ Wokonda vinyo ndi mafuta sadzapeza chuma.+

18 Munthu woipa ndiye dipo la wolungama,+ ndipo munthu wochita zachinyengo amalowa m’malo mwa anthu owongoka mtima.+

19 Kuli bwino kukhala m’chipululu kusiyana ndi kukhala mokhumudwa ndi mkazi wolongolola.+

20 Chuma chosiririka ndiponso mafuta zimakhala pamalo a munthu wanzeru,+ koma wopusa amazimeza.+

21 Amene akufunafuna chilungamo+ ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+

22 Wanzeru amakwera mzinda wa anthu amphamvu, kuti athetse mphamvu imene mzindawo umadalira.+

23 Wosunga pakamwa pake ndiponso lilime lake akuteteza moyo wake ku masautso.+

24 Munthu amene amadzikuza akapsa mtima, amatchedwa wodzikuza, wonyada ndi wodzitama.+

25 Zolakalaka za munthu waulesi zidzamupha, chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+ 26 Tsiku lonse amaoneka kuti akulakalaka kwambiri chinachake, koma wolungama amapatsa ndipo saumira chilichonse.+

27 Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+

28 Mboni yonama idzawonongedwa,+ koma munthu amene amamvetsera adzalankhula kwamuyaya.+

29 Munthu woipa amakhala ndi nkhope yamwano,+ koma wowongoka mtima ndi amene njira zake zidzakhazikike.+

30 Palibe nzeru kapena kuzindikira kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.+

31 Hatchi* anaikonzera tsiku la nkhondo,+ koma Yehova ndiye amapulumutsa.+

22 Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.+ Kulemekezedwa kuli bwino kuposa siliva ndi golide.+

2 Munthu wolemera ndiponso munthu wosauka n’chimodzimodzi.+ Amene anapanga onsewa ndi Yehova.+

3 Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala,+ koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.+

4 Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.+

5 Minga ndi misampha zimakhala m’njira ya munthu wochita zopotoka,+ koma woteteza moyo wake amakhala nazo kutali.+

6 Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.+ Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.+

7 Wolemera ndi amene amalamulira anthu osauka,+ ndipo wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.+

8 Wofesa zosalungama adzakolola zopweteka,+ ndipo ndodo ya ukali wake idzatha.+

9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+

10 Thamangitsa wonyoza, kuti mikangano ithe ndiponso kuti milandu ndi kunyozedwa zilekeke.+

11 Amene amakondwera kukhala ndi mtima woyera+ ndiponso amene mawu ake ndi okopa, adzakhala bwenzi la mfumu.+

12 Maso a Yehova amateteza wodziwa zinthu,+ koma iye amawononga mawu a munthu wochita zachinyengo.+

13 Waulesi amati:+ “Panja pali mkango!+ Ndithu undipha pakati pa bwalo la mzinda!”

14 Pakamwa pa akazi achilendo pali ngati dzenje lakuya.+ Wotsutsidwa ndi Yehova adzagweramo.+

15 Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.+ Koma ndodo yomulangira* ndi imene imauthamangitsira kutali ndi iye.+

16 Amene amabera mwachinyengo munthu wonyozeka kuti apeze zinthu zambiri,+ komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera, ndithu adzasauka.+

17 Tchera khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzeru,+ kuti ulandire ndi mtima wonse nzeru zochokera kwa ine.+ 18 Pakuti n’chinthu chosangalatsa kuti uzisunge mumtima mwako,+ kuti zikhazikike pamilomo yako.+

19 Lero ndakudziwitsa zinthu,+ kuti uzidalira Yehova.

20 Kodi sindinakulembere zinthu zolangiza ndi zophunzitsa,+ 21 n’cholinga chakuti ndikusonyeze kudalirika kwa mawu oona, kuti uthe kubwezera mawu oonadi kwa amene wakutuma?+

22 Usabere munthu wonyozeka chifukwa chakuti ndi wonyozeka,+ ndipo usapondereze wosautsika pachipata cha mzinda.+ 23 Pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+ ndipo adzalanda moyo wa amene akuwabera.+

24 Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya,+ ndipo usamayende ndi munthu waukali, 25 kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.+

26 Usakhale pakati pa anthu ogwirana chanza,+ pakati pa anthu amene amakhala chikole cha ngongole za anthu ena.+ 27 Ukadzalephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi limene umagonapo.

28 Usasunthire kumbuyo malire akalekale, amene makolo ako anaika.+

29 Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu.+ Sadzaima pamaso pa anthu wamba.

23 Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uzionetsetsa zimene zili pamaso pako,+ 2 ndipo uzidziletsa* ngati uli wadyera.+ 3 Usasonyeze kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma, chifukwa ndi zakudya zachinyengo.+

4 Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.+ Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.+ 5 Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka?+ Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.+

6 Usamadye chakudya cha aliyense womana,+ kapena kusonyeza kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma.+ 7 Pakuti iye ali ngati munthu amene wawerengetsera bwino zinthu mumtima mwake. Amakuuza kuti:+ “Idya, imwa,” koma salankhula ndi mtima wonse.+ 8 Nthongo imene wadya udzaisanza, ndipo mawu ako abwino adzakhala atapita pachabe.+

9 Usalankhule m’makutu mwa munthu wopusa,+ chifukwa iye adzanyoza mawu ako anzeru.+

10 Usasunthire kumbuyo malire akalekale,+ ndipo usalowe m’munda mwa ana amasiye.*+ 11 Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+

12 Bweretsa mtima wako kuti umve malangizo, ndi khutu lako kuti limve mawu a munthu wodziwa zinthu.+

13 Usam’mane chilango* mwana.+ Ngakhale utam’kwapula ndi chikwapu, sangafe ayi. 14 Um’kwapule ndi chikwapu, kuti upulumutse moyo wake ku Manda.+

15 Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,+ ndithu mtima wanga udzasangalala.+ 16 Impso zanga zidzasangalala milomo yako ikamalankhula zowongoka.+

17 Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+ koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+ 18 Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+ ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+

19 Iwe mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru, ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino.+

20 Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri,+ ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka.+ 21 Chifukwa chidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka,+ ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.+

22 Mvera bambo ako amene anakubereka,+ ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ 23 Gula choonadi+ ndipo usachigulitse. Gula nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.+ 24 Bambo wa munthu wolungama ndithu adzasangalala.+ Bambo wobereka mwana wanzeru adzakondwera naye.+ 25 Bambo ako ndi mayi ako adzakondwera, ndipo mayi amene anakubereka adzasangalala.+

26 Mwana wanga, ndipatse mtima wako, ndipo maso ako asangalale ndi njira zanga.+ 27 Pakuti hule lili ngati dzenje lakuya,+ ndipo mkazi wachilendo ali ngati chitsime chopapatiza. 28 Ndithudi iye mofanana ndi wachifwamba,+ amabisalira anthu panjira, ndipo amachulukitsa amuna achinyengo.+

29 Ndani ali ndi tsoka? Ndani sakhazikika maganizo? Ndani ali pa mikangano?+ Ndani ali ndi nkhawa? Ndani ali ndi zilonda popanda chifukwa? Ndani ali ndi maso ofiira? 30 Ndi anthu amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo,+ amene amabwera kudzafunafuna vinyo wosakaniza.+ 31 Usayang’ane vinyo akamaoneka wofiira, akamanyezimira m’kapu, akamatsetserekera kukhosi mwamyaa! 32 Kumapeto kwake amaluma ngati njoka,+ ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri.+ 33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo, ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota.+ 34 Ndithu udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja, komanso ngati munthu amene wagona pamwamba pa mlongoti wa ngalawa.+ 35 Udzati: “Andimenya koma sindinavulale, andikuntha koma sindinadziwe. Kodi ndidzuka nthawi yanji+ kuti ndikamwenso wina?”+

24 Usamasirire anthu oipa,+ ndipo usamasonyeze kuti ukusirira kukhala pagulu lawo,+ 2 chifukwa mtima wawo umangokhalira kuganizira zolanda zinthu za ena, ndipo milomo yawo imangokhalira kunena zobweretsera ena mavuto.+

3 Nzeru zimamanga banja la munthu,+ ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.+ 4 Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda zamkati mwa nyumba zidzaze ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+

5 Munthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwanzeru ndiye mwamuna wamphamvu,+ ndipo munthu wodziwa zinthu amachulukitsa mphamvu zake.+ 6 Iweyo udzatha kumenya nkhondo yako potsatira malangizo anzeru,+ ndipo pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+

7 Kwa munthu wopusa, nzeru zenizeni n’chinthu chapatali.+ Iye satsegula pakamwa pake pachipata cha mzinda.

8 Aliyense wokonzera anzake ziwembu adzatchedwa katswiri wa maganizo oipa.+

9 Khalidwe lotayirira lobwera chifukwa cha kupusa limakhala tchimo,+ ndipo munthu wonyoza, anthu amanyansidwa naye.+

10 Ukafooka pa tsiku la masautso,+ mphamvu zako zidzakhala zochepa.

11 Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe, ndipo amene akudzandira popita ku imfa, chonde uwabweze.+ 12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+

13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino, ndipo uchi wotsekemera wochokera pazisa za njuchi uuike m’kamwa mwako.+ 14 M’njira yomweyo, dziwa nzeru kuti upindule.+ Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+

15 Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pamalo ake okhala.+ Usamasakaze malo ake okhala,+ 16 pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.+ Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa.+

17 Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere,+ 18 kuti Yehova angaone ndipo zingamuipire m’maso mwake n’kuchotsa mkwiyo wake pamdani wakoyo.+

19 Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa. Usamasirire anthu oipa,+ 20 pakuti aliyense woipa alibe tsogolo,+ ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+

21 Mwana wanga uziopa Yehova ndiponso mfumu.+ Usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+ 22 pakuti tsoka lawo lidzagwa mwadzidzidzi,+ ndipo ndani angadziwe za kufafanizika kwa anthu ofuna kuti zinthu zisinthe?+

23 Mawu awanso akupita kwa anthu anzeru:+ Si bwino kukondera poweruza.+

24 Munthu amene amauza woipa kuti: “Ndiwe wolungama,”+ anthu adzamutemberera, ndipo mitundu ya anthu idzamutsutsa. 25 Koma anthu omudzudzula zinthu zidzawayendera bwino,+ ndipo adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+ 26 Woyankha mosapita m’mbali adzapsompsona milomo ya anthu.+

27 Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo konza munda wako.+ Ukatero ukamange banja lako.

28 Usakhale mboni yotsutsana ndi mnzako popanda umboni,+ chifukwa ukhoza kukhala wopusa ndi milomo yako.+ 29 Usanene kuti: “Ndim’chitira zimene iye anandichitira.+ Aliyense ndizim’bwezera mogwirizana ndi zimene anachita.”+

30 Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi+ ndiponso pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+ 31 Ndipo ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.+ Zitsamba zoyabwa zinali paliponse m’mundamo komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+

32 Choncho ine nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,+ ndipo ndinaphunzirapo* kuti:+ 33 Ukati, “Ndigoneko pang’ono, ndibeko katulo pang’ono, ndipindeko manja pang’ono pogona,”+ 34 umphawi wako ndithu udzabwera ngati wachifwamba ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

25 Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya mfumu ya Yuda+ anakopa, ndi iyi:

2 Ulemerero wa Mulungu ndiwo kusunga chinsinsi,+ ndipo ulemerero wa mafumu ndiwo kufufuza bwino nkhani.+

3 Kutalika kwa kumwamba,+ kuzama kwa dziko lapansi,+ ndiponso mtima wa mafumu, zonsezi n’zosatheka kuzifufuza.+

4 Siliva akachotsedwa zotsalira pomuyenga, yense adzatuluka woyengeka bwino.+

5 Woipa akachotsedwa pamaso pa mfumu,+ mpando wake wachifumu udzakhazikitsidwa ndi chilungamo.+

6 Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+ ndipo usaime pamalo a anthu olemekezeka,+ 7 pakuti ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti: “Bwera pamwamba pano,”+ kusiyana n’kuti ikutsitse pamaso pa munthu wolemekezeka amene wamuona ndi maso ako.+

8 Usamapite kukazenga mlandu mofulumira, pakuti udzachita chiyani pamapeto pake mnzakoyo akakuchititsa manyazi?+ 9 Kambirana mlandu wako ndi mnzako,+ ndipo usaulule chinsinsi cha munthu wina,+ 10 kuti amene akumvetsera angakuchititse manyazi ndiponso kuti nkhani yoipa imene iwe wanena ingavute kuiiwala.

11 Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.+

12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo* yagolide, ndiponso ngati chokongoletsera chagolide wapadera.+

13 Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aituma ili ngati kuzizira kwa chipale chofewa+ pa tsiku lokolola, chifukwa imatsitsimula moyo wa ambuye ake.+

14 Munthu wodzitama kuti wapereka mphatso koma sanapereke, ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.+

15 Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.+

16 Ukapeza uchi udye wokukwanira,+ kuti usadye wambiri n’kuusanza.+

17 Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako, kuti angatope nawe n’kuyamba kudana nawe.

18 Munthu wonenera mnzake umboni wonama ali ngati chibonga cha kunkhondo, lupanga, ndi muvi wakuthwa.+

19 Kudalira munthu amene amachita zachinyengo pa tsiku la masautso kuli ngati dzino lothyoka ndi phazi lotsimphina.+

20 Wovula malaya pa tsiku lozizira ali ngati vinyo wowawasa wothiridwa mu soda, ndiponso ngati woimbira nyimbo munthu wa mtima wachisoni.+

21 Ngati munthu wodana nawe ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse madzi akumwa,+ 22 pakuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,+ ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.+

23 Mphepo yochokera kumpoto imabweretsa mvula yambiri. Imakhala ngati kuti yabereka mvulayo ndi ululu wa pobereka.+ Chotero munthu wa lilime loulula chinsinsi amakhala ndi nkhope yonyozedwa.+

24 Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba, kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+

25 Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+ ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.+

26 Munthu wolungama akamanjenjemera pamaso pa munthu woipa, amakhala ngati kasupe woipitsidwa ndiponso chitsime chowonongedwa.+

27 Kudya uchi wambiri si bwino,+ ndipo anthu akamafunafuna okha ulemerero, kodi umenewo ndi ulemererodi?+

28 Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.+

26 Monga chipale chofewa m’chilimwe ndiponso mvula pa nthawi yokolola,+ momwemonso ulemerero suyenerera munthu wopusa.+

2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira, ndiponso namzeze* amakhala ndi chifukwa choulukira. Momwemonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.+

3 Chikwapu n’cha hatchi,+ zingwe n’za pakamwa pa bulu,+ ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+

4 Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti iweyo usafanane naye.+

5 Uzimuyankha wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti asadzione ngati wanzeru m’maso mwake.+

6 Munthu amene amakankhira nkhani m’manja mwa wopusa ali ngati munthu wopundula mapazi ake, ndiponso ngati munthu amene amamwa chiwawa.+

7 Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati munthu wa miyendo yolumala amene wasenza madzi.+

8 Munthu amene amapereka ulemerero kwa munthu wopusa ali ngati munthu wobisa mwala pamulu wa miyala.+

9 Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati chitsamba chaminga m’manja mwa munthu woledzera.+

10 Wolemba ntchito munthu wopusa kapena munthu wongodutsa m’njira, ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa chilichonse.+

11 Monga galu amene wabwerera ku masanzi ake, wopusa amabwereza uchitsiru wake.+

12 Kodi waona munthu wodziona ngati wanzeru m’maso mwake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu+ kuposa iyeyo.

13 Waulesi amati: “Panjira pali mkango wamphamvu. M’mabwalo a mzinda mukuyendayenda mkango.”+

14 Chitseko chimazungulira pomwe anachimangirira, ndipo waulesi amangotembenukatembenuka pabedi pake.+

15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera, koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa amaona kuti n’zotopetsa kwambiri.+

16 Waulesi amadziona kuti ndi wanzeru kwambiri m’maso mwake+ kuposa anthu 7 oyankha zanzeru.

17 Munthu wongodutsa amene amalowerera mkangano womwe si wake n’kukwiya nawo, ali ngati munthu wogwira makutu a galu.+

18 Monga munthu wamisala amene akuponya zida ndiponso mivi yamoto+ yakupha, 19 ndi mmenenso alili munthu amene amapusitsa mnzake, n’kunena kuti: “Inetu ndimangochita zocheza.”+

20 Popanda nkhuni moto umazima, ndipo popanda munthu wonenera anzake zoipa mikangano imazilala.+

21 Monga mmene amakhalira makala pamoto wonyeka ndiponso nkhuni pamoto woyaka, ndi mmenenso amakhalira munthu wokonda kuyambana ndi anthu pokolezera mikangano.+

22 Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga, zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+

23 Milomo yonena zabwino mwachiphamaso koma mumtima muli zoipa, ili ngati siliva wokutira phale.+

24 Munthu wodana nawe amadzibisa ndi milomo yake, koma mkati mwake mumakhala chinyengo.+ 25 Ngakhale azilankhula mawu okoma,+ usam’khulupirire+ chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.+ 26 Chidani chimaphimbidwa ndi chinyengo. Zoipa zake zidzaululika mumpingo.+

27 Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,+ ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye.+

28 Lilime lonama limadana ndi amene lam’pweteka,+ ndipo pakamwa polankhula zabwino mokokomeza pamabweretsa chiwonongeko.+

27 Usadzitame ndi zamawa+ chifukwa sukudziwa zimene zidzachitike mawa.+

2 Mlendo akutamande, osati pakamwa pako. Munthu wochokera kudziko lina achite zimenezo, osati milomo yako.+

3 Mwala umalemera ndiponso mchenga umalemera ukaunyamula,+ koma kusautsa kwa munthu wopusa kumalemera kwambiri kuposa zonsezi.+

4 Mkwiyo umasefukira ndipo ukali ndi wankhanza,+ koma nsanje ndani angaipirire?+

5 Kudzudzula munthu mosabisa mawu, kuli bwino+ kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho.

6 Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika,+ koma kuti munthu wodana nawe akupsompsone pamafunika kumuchonderera.+

7 Munthu akakhuta amapondaponda uchi wa kuchisa, koma kwa munthu wanjala chinthu chilichonse chowawa chimatsekemera.+

8 Monga mbalame imene ikuthawa pachisa pake,+ ndi mmenenso amakhalira munthu amene akuthawa kwawo.+

9 Mafuta ndi zofukiza zonunkhira+ n’zimene zimasangalatsa mtima, chimodzimodzinso kukoma kwa mnzako chifukwa cha malangizo ake ochokera pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.+

10 Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako, ndipo usalowe m’nyumba ya m’bale wako pa tsiku limene tsoka lakugwera. Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa m’bale wako amene ali kutali.+

11 Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga,+ kuti ndimuyankhe amene akunditonza.+

12 Wochenjera amene waona tsoka amabisala.+ Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.+

13 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo,+ umulande chovala chake. Ndiponso wochita zoipa ndi mkazi wachilendo umulande chikole.+

14 Munthu amene amadalitsa mnzake mokuwa m’mawa kwambiri, anthu adzamuona ngati akutemberera.+

15 Denga lodontha limene limathawitsa munthu pa tsiku la mvula yosalekeza, limafanana ndi mkazi wolongolola.+ 16 Aliyense wobisa mkaziyo wabisa mphepo, ndipo dzanja lake lamanja limagwira mafuta.

17 Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.+

18 Amene akuteteza mtengo wa mkuyu adzadya zipatso zake,+ ndipo amene akuteteza mbuye wake adzalemekezedwa.+

19 Monga momwe nkhope imaonekera chithunzi chake m’madzi, momwemonso mtima wa munthu umaonekera mumtima wa munthu wina.

20 Manda ndiponso malo a chiwonongeko+ sakhuta.+ Nawonso maso a munthu sakhuta.+

21 Siliva amamuyengera m’mbiya yoyengera+ ndipo golide amamuyengera m’ng’anjo,+ momwemonso chitamando choperekedwa kwa munthu chimasonyeza mmene iye alili.+

22 Ngakhale utasinja chitsiru mumtondo ndi musi limodzi ndi mbewu, uchitsiru wake sungachichokere.+

23 Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako. Ika mtima wako pa magulu a ziweto zako,+ 24 pakuti chuma sichidzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo chisoti chachifumu sichidzakhalapo ku mibadwo yonse.

25 Udzu wobiriwira wapita, udzu watsopano waoneka, ndipo zomera za m’mapiri zasonkhanitsidwa.+ 26 Nkhosa zamphongo zazing’ono zimakupezetsa zovala,+ ndipo mbuzi zamphongo ndizo malipiro ogulira munda. 27 Pali mkaka wa mbuzi wokwanira woti udye, woti ukhale chakudya cha banja lako, ndiponso wopezera zofunika+ za pa moyo wa atsikana ako.

28 Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,+ koma olungama ali ngati mkango wamphamvu umene umakhala wolimba mtima.+

2 Anthu okhala m’dziko akamachimwa pamakhala akalonga ambiri otsatizanatsatizana,+ koma chifukwa cha munthu wozindikira, wodziwa zinthu zoyenera kuchita, kalonga amakhala kwa nthawi yaitali.+

3 Mwamuna wamphamvu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+ ali ngati mvula imene imakokolola zinthu moti sipakhalanso chakudya.

4 Anthu osiya chilamulo akamatamanda munthu woipa,+ anthu amene amasunga chilamulo amawaukira.+

5 Anthu okonda kuchita zoipa sangamvetse chilungamo, koma amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.+

6 Munthu wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika, ali bwino kuposa munthu aliyense woyenda m’njira zokhota, ngakhale ali wolemera.+

7 Mwana womvetsa zinthu amasunga malamulo,+ koma wochita ubwenzi ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+

8 Munthu amene amachulukitsa zinthu zamtengo wapatali kuchokera ku chiwongoladzanja ndi katapira,*+ amangosungira zinthuzo munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+

9 Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo,+ ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+

10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima+ kuti ayende m’njira yoipa, adzagwera m’dzenje lake lomwe.+ Koma anthu osalakwa adzapeza zabwino.+

11 Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru m’maso mwake,+ koma munthu wonyozeka amene ali wozindikira zinthu amam’fufuza n’kudziwa zoona zake.+

12 Anthu olungama akamasangalala+ zimakhala bwino kwambiri, koma anthu oipa akamalamulira, munthu amadzisintha maonekedwe.+

13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+

14 Wodala ndi munthu amene amaopa Mulungu nthawi zonse,+ koma woumitsa mtima wake adzagwera m’tsoka.+

15 Mtsogoleri woipa wolamulira anthu onyozeka ali ngati mkango wobangula ndiponso chimbalangondo chimene chikubwera kudzakuluma.+

16 Mtsogoleri amene ali wosazindikira kwenikweni amakhalanso wakatangale kwambiri,+ koma munthu wodana ndi phindu lachinyengo+ adzachulukitsa masiku ake.

17 Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse.

18 Woyenda mosalakwa adzapulumutsidwa,+ koma woyenda m’njira zokhota adzagwa mwadzidzidzi.+

19 Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+ ndipo amene amafunafuna zinthu zopanda phindu adzakhala ndi umphawi waukulu.+

20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+

21 Si bwino kukondera.+ Si bwinonso kuti mwamuna wamphamvu achimwe chifukwa cha kachidutswa ka mkate.

22 Munthu wanjiru amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali,+ koma sadziwa kuti umphawi udzamugwera.

23 Wodzudzula munthu,+ patsogolo pake adzakondedwa kwambiri kuposa amene amakokomeza ndi lilime lake ponena zinthu zabwino za wina.

24 Wobera bambo ake ndi mayi ake+ n’kumanena kuti: “Si kulakwa,”+ amakhala mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.

25 Munthu wonyada amayambitsa mikangano,+ koma wodalira Yehova adzanenepa.+

26 Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa,+ koma woyenda mwanzeru ndi amene adzapulumuke.+

27 Wopatsa zinthu munthu wosauka sadzasowa kanthu,+ koma wophimba maso ake adzapeza matemberero ambiri.+

28 Oipa akamalamulira, munthu amadzibisa.+ Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+

29 Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+

2 Olungama akachuluka, anthu amasangalala,+ koma aliyense woipa akayamba kulamulira, anthu amabuula.+

3 Munthu wokonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+ koma woyenda ndi mahule amawononga zinthu zamtengo wapatali.+

4 Pochita zinthu zachilungamo, mfumu imachititsa dziko kulimba,+ koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.+

5 Mwamuna wamphamvu amene amanena zabwino za mnzake mokokomeza,+ akuyalira ukonde mapazi ake.+

6 Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+ koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+

7 Wolungama amaganizira za mlandu wa anthu onyozeka.+ Woipa saganizira zimenezo.+

8 Anthu olankhula modzitama amabutsa mkwiyo wa mzinda,+ koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+

9 Munthu wanzeru akakhala pa mlandu ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso n’kumaseka, ndipo munthu wanzeruyo sapeza mpumulo.+

10 Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi aliyense wopanda cholakwa,+ koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.+

11 Wopusa amatulutsa mkwiyo* wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.+

12 Mtsogoleri akamamvera mabodza, onse omutumikira adzakhala oipa.+

13 Munthu wosauka ndiponso munthu wozunza ena n’chimodzimodzi,+ koma Yehova amawalitsa maso a onsewa.+

14 Mfumu ikamaweruza anthu onyozeka mwachilungamo,+ mpando wake wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.+

15 Chikwapu ndi chidzudzulo n’zimene zimapereka nzeru,+ koma mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.+

16 Oipa akachuluka, machimo amachuluka, koma olungama adzawaona oipawo akugwa.+

17 Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumulo ndiponso adzasangalatsa kwambiri moyo wako.+

18 Popanda kutsogozedwa ndi Mulungu, anthu amatayirira,+ koma odala ndi amene amasunga malamulo.+

19 Wantchito salola kusintha ndi mawu okha,+ chifukwa amamvetsa koma satsatira.+

20 Kodi waona munthu wopupuluma m’mawu ake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.+

21 Ngati munthu akusasatitsa* wantchito wake kuyambira ali mwana, akadzakula adzakhala wosayamika.

22 Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano,+ ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+

23 Kudzikuza kwa munthu wochokera kufumbi kudzamutsitsa,+ koma wa mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+

24 Wochita ubwenzi ndi mbala akudana ndi moyo wake.+ Iye angamve lumbiro lokhudza temberero, koma osakanena chilichonse.+

25 Kuopa anthu n’kumene kumatchera msampha,+ koma wokhulupirira Yehova adzatetezedwa.+

26 Anthu ambiri amafuna kuonana ndi mtsogoleri,+ koma chiweruzo cha munthu chimachokera kwa Yehova.+

27 Munthu wopanda chilungamo amakhala wonyansa kwa anthu olungama,+ ndipo munthu wowongoka m’njira yake amakhala wonyansa kwa munthu woipa.+

30 Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake, mwamuna wamphamvu. Mawuwa anali uthenga wamphamvu+ womwe iye analankhula ndi Itiyeli, ndi Itiyeli ndiponso Ukali, kuti:

2 Ine ndine wopanda nzeru kuposa munthu wina aliyense,+ ndipo sindimvetsa zinthu monga mmene anthu onse amamvetsetsera.+ 3 Inetu ndilibe nzeru,+ ndipo sindidziwa nzeru zimene zili ndi Woyera Koposa.+

4 Ndani amene anakwerapo kumwamba n’kubwerako?+ Ndani anasonkhanitsapo mphepo m’manja mwake?+ Ndani anamangapo madzi munsalu?+ Ndani anaika malekezero onse a dziko lapansi?+ Dzina lake ndani?+ Nanga mwana wake dzina lake ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.+

5 Mawu alionse a Mulungu ndi oyera.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ 6 Usawonjezere kanthu pa mawu ake+ kuti angakudzudzule ndiponso kuti ungakhale wabodza.+

7 Ndikukupemphani zinthu ziwiri.+ Musandikanize ndisanafe.+ 8 Zachinyengo ndi mawu onama muwaike kutali ndi ine.+ Musandipatse umphawi kapena chuma.+ Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya,+ 9 kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani+ kuti: “Kodi Yehova ndani?”+ ndiponso kuti ndisasauke n’kukaba ndi kunyozetsa dzina la Mulungu wanga.+

10 Usanenere wantchito zoipa kwa mbuye wake,+ kuti angakutemberere ndiponso kuti ungakhale ndi mlandu.+

11 Pali m’badwo umene umatemberera ngakhale abambo awo ndiponso umene sudalitsa ngakhale amayi awo.+

12 Pali m’badwo umene umadziona kuti ndi woyera,+ koma sunasambe kuti uchotse ndowe zake.+

13 Pali m’badwo umene maso ake ali pamwamba kwambiri, ndiponso umene maso ake owala ali odzikweza.+

14 Pali m’badwo umene mano ake ali ngati malupanga ndiponso umene nsagwada zake zili ngati mipeni yophera nyama,+ kuti m’badwowo udye osautsidwa onse a padziko lapansi ndiponso anthu osauka pakati pa anthu.+

15 Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti: “Tipatseni! Tipatseni!” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta ndiponso zinthu zinayi zimene sizinena kuti: “Ndakhuta!” Zinthuzo ndi izi: 16 Manda,+ mimba yosabereka,+ nthaka imene sikhuta madzi,+ ndiponso moto+ umene sunena kuti: “Ndakhuta!”+

17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.

18 Pali zinthu zitatu zimene n’zodabwitsa kwambiri kwa ine, ndiponso zinthu zinayi zimene sindizimvetsa. Zinthuzo ndi izi: 19 Njira ya chiwombankhanga m’mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakatikati pa nyanja,+ ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.+

20 Nayi njira ya mkazi wachigololo: Iye amadya n’kupukuta pakamwa pake ndipo amanena kuti: “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+

21 Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansi ndiponso zinthu zinayi zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthuzo ndi izi: 22 Kapolo akamalamulira monga mfumu,+ munthu wopusa akakhuta,+ 23 mkazi wodedwa akakwatiwa,+ ndiponso mtsikana wantchito akatenga malo a mbuye wake wamkazi.+

24 Pali zinthu zinayi zomwe ndi zing’onozing’ono kwambiri padziko lapansi koma n’zanzeru mwachibadwa:+ 25 Nyerere si zamphamvu,+ koma zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe.+ 26 Mbira+ si nyama zamphamvu koma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+ 27 Dzombe+ lilibe mfumu koma limauluka lonse litagawikana m’magulumagulu.+ 28 Nalimata*+ amagwira zinthu ndi manja ake ndipo amapezeka m’nyumba yaikulu yachifumu.

29 Pali zinthu zitatu zimene zimayenda molemekezeka ndiponso zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira. Zinthuzo ndi izi: 30 Mkango, umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire ndiponso umene suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo,+ 31 galu wosaka kapena mbuzi yamphongo, ndiponso mfumu imene ikutsogolera asilikali ake.+

32 Ngati wachita zinthu zopusa n’kudzikweza,+ ndiponso ngati watsimikiza mtima wako kuti uchite zimenezo, gwira pakamwa pako.+ 33 Pakuti mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta, mphuno ukaifinya imatulutsa magazi, ndipo kutulutsa mkwiyo kumayambitsa mkangano.+

31 Mawu a Mfumu Lemueli, uthenga wamphamvu+ umene mayi ake anamupatsa pomuphunzitsa:+

2 Kodi ndikufuna ndikuuze chiyani mwana wanga? Kodi ndikufuna ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera m’mimba mwanga?+ Kodi ndikufuna ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+

3 Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+ ndipo usamapereke njira zako ku zinthu zimene zimachititsa mafumu kufafanizidwa.+

4 N’kosayenera kwa mafumu iwe Lemueli, n’kosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,+ kapena kuti akuluakulu olemekezeka azinena kuti: “Kodi chakumwa choledzeretsa chili kuti?” 5 Chifukwa angamwe n’kuiwala malamulo ndi kupondereza ufulu wa ana ovutika.+ 6 Anthu inu, perekani chakumwa choledzeretsa kwa munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa+ ndi vinyo kwa anthu amene mtima wawo ukuwawa.+ 7 Munthu amwe n’kuiwala umphawi wake, ndipo asakumbukirenso mavuto ake.

8 Tsegula pakamwa pako kuti ulankhulire munthu amene sangathe kudzilankhulira yekha,+ kuti uthandize onse amene atsala pang’ono kufa.+ 9 Tsegula pakamwa pako, weruza mwachilungamo ndipo thandiza munthu wosautsika ndi wosauka pa mlandu wake.+

א [ʼAʹleph]

10 Mkazi wabwino, ndani angam’peze?+ Mtengo wake umaposa wa miyala yamtengo wapatali.

ב [Behth]

11 Mtima wa mwamuna wake* umamudalira, ndipo mwamunayo sasowa kalikonse.+

ג [Giʹmel]

12 Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amapatsa mwamuna wakeyo zabwino osati zoipa.+

ד [Daʹleth]

13 Amafunafuna ulusi ndi nsalu, ndipo manja ake amagwira ntchito iliyonse mosangalala.+

ה [Heʼ]

14 Iye ali ngati ngalawa za munthu wamalonda.+ Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali.

ו [Waw]

15 Amadzukanso kudakali usiku,+ n’kupereka chakudya kwa banja lake ndipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+

ז [Zaʹyin]

16 Amakaona munda n’kuugula.+ Amalima munda wa mpesa chifukwa cha ntchito ya manja ake.+

ח [Chehth]

17 Amakhala wokonzeka kugwira ntchito yolimba, ndipo amalimbitsa manja ake.+

ט [Tehth]

18 Amaona kuti malonda ake akuyenda bwino. Nyale yake siizima usiku.+

י [Yohdh]

19 Amatambasulira manja ake ndodo yokulungako ulusi, ndipo manja ake amagwira ndodo yopotera chingwe.+

כ [Kaph]

20 Amatambasulira dzanja lake munthu wosautsika, ndipo manja ake amawatambasulira munthu wosauka.+

ל [Laʹmedh]

21 Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lake chifukwa a m’banja lake onse amavala zovala zotentha.*+

מ [Mem]

22 Iye amadzipangira zoyala pabedi.+ Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira.+

נ [Nun]

23 Mwamuna wake*+ amadziwika pazipata,+ akakhala pansi pamodzi ndi akulu a m’dzikolo.

ס [Saʹmekh]

24 Iye amapanga zovala zamkati+ n’kuzigulitsa, ndipo amapanga malamba n’kuwapereka kwa amalonda.

ע [ʽAʹyin]

25 Mphamvu ndi ulemerero ndiye zovala zake,+ ndipo sada nkhawa akamaganizira zam’tsogolo.+

פ [Peʼ]

26 Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+ ndipo lamulo la kukoma mtima kosatha lili palilime lake.+

צ [Tsa·dhehʹ]

27 Iye amayang’anira zochitika za pabanja pake, ndipo sadya chakudya cha ulesi.+

ק [Qohph]

28 Ana ake amaimirira n’kumuuza kuti ndi wodala.+ Mwamuna wake amaimirira n’kumutamanda kuti:+

ר [Rehsh]

29 “Pali ana aakazi ambiri+ amene asonyeza kuti ndi akazi abwino, koma iweyo waposa onsewo.”+

ש [Shin]

30 Chikoka chikhoza kukhala chachinyengo+ ndipo kukongola kukhoza kukhala kopanda phindu,+ koma mkazi woopa Yehova ndi amene amatamandidwa chifukwa cha zochita zake.+

ת [Taw]

31 M’patseni zipatso za manja ake,+ ndipo ntchito zake zimutamande ngakhale m’zipata.+

Mawu a chinenero choyambirira amene tawamasulira kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

M’Baibulo, mawu akuti “chitsiru” amatanthauza munthu amene amaphwanya dala mfundo za Mulungu.

Onani Zakumapeto 5.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “zimene unazipeza ukumva kupweteka.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Pawindo” limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.

Ena amati “wanthota.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Ena amati “mphafa.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

M’Chiheberi, nzeru akuitenga ngati munthu wamkazi m’chaputala chino.

Ena amati “amanzuna.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Zingatanthauzenso kuvomerezedwa ndi anthu.

Mawu ake enieni, “wa mzimu wokhulupirika.”

“Chipini” ndi kachitsulo kapena kamtengo kokongoletsera kamene amakaika pabowo limene amaboola pamphuno.

Zingatanthauzenso kuvomerezedwa ndi anthu.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “mwiniwake.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “alibe mtima.”

Kapena kuti “tsindwi.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “uziika mpeni pakhosi pako.”

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Ena amati “masikiyo.”

Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.

Mawu ake enieni, “mzimu.”

Munthu wosasatitsidwa ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.

“Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala m’madzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama n’kumayamwa magazi.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

“Nalimata” ndi kabuluzi kakang’ono komwe kamakonda kukhala m’nyumba, koonekera matumbo.

Mawu ake enieni, “mwiniwake.”

Mawu ake enieni, “zovala ziwiri.”

Mawu ake enieni, “mwiniwake.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena