Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Ezra 1:1-10:44
  • Ezara

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ezara
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Ezara

Ezara

1 M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, Yehova analimbikitsa+ mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa+ mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti:

2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti,+ ‘Yehova Mulungu wakumwamba+ wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu+ m’dziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+ 4 Aliyense amene akukhala monga mlendo+ kumalo alionse, anthu akwawo amuthandize ndi siliva, golide, katundu, ziweto, limodzi ndi nsembe yaufulu+ ya nyumba ya Mulungu woona, yomwe inali ku Yerusalemu.’”

5 Ndiyeno atsogoleri+ a mabanja a fuko la Yuda, la Benjamini, ansembe, ndi Alevi, aliyense amene Mulungu woona analimbikitsa mtima wake,+ ananyamuka kuti apite kukamanganso nyumba ya Yehova,+ yomwe inali ku Yerusalemu. 6 Anthu onse okhala nawo pafupi anawathandiza*+ powapatsa ziwiya zasiliva, golide, katundu, ziweto, ndi zinthu zabwinozabwino, kuwonjezera pa zonse zimene zinaperekedwa mwaufulu.+

7 Komanso, Mfumu Koresi inabweretsa ziwiya za nyumba ya Yehova.+ Ziwiyazo n’zimene Nebukadinezara anatenga ku Yerusalemu+ n’kukaziika m’kachisi wa mulungu wake.+ 8 Koresi mfumu ya Perisiya anatuma msungichuma Mitiredati yemwe anabweretsa ziwiyazo n’kuziwerenga. Atatero anazipereka kwa Sezibazara*+ mtsogoleri wa Yuda.+

9 Ziwiyazo zinali zochuluka chonchi: ziwiya 30 zagolide zooneka ngati mabasiketi, ziwiya 1,000 zasiliva zooneka ngati mabasiketi, ndi ziwiya 29 zowonjezera. 10 Panalinso mbale 30 zing’onozing’ono zolowa+ zagolide, mbale 410 zing’onozing’ono zolowa zasiliva zogwiritsira ntchito zina, ndi ziwiya zina 1,000. 11 Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400 ndipo Sezibazara+ anabweretsa zonsezi ku Yerusalemu. Anatenganso anthu amene anagwidwa ukapolo+ kuchoka nawo ku Babulo n’kupita nawo ku Yerusalemu.

2 Awa ndiwo anali anthu a m’chigawo*+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera+ ku Babulo. Anthuwa anabwerera+ ku Yerusalemu ndi ku Yuda,+ aliyense kumzinda wakwawo. 2 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya,+ Reelaya, Moredekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, ndi Bana.

Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi: 3 Ana a Parosi,+ 2,172. 4 Ana a Sefatiya,+ 372. 5 Ana a Ara,+ 775. 6 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,812. 7 Ana a Elamu,+ 1,254. 8 Ana a Zatu,+ 945. 9 Ana a Zakai,+ 760. 10 Ana a Bani,+ 642. 11 Ana a Bebai,+ 623. 12 Ana a Azigadi,+ 1,222. 13 Ana a Adonikamu,+ 666. 14 Ana a Bigivai,+ 2,056. 15 Ana a Adini,+ 454. 16 Ana a Ateri,+ a m’nyumba ya Hezekiya, 98. 17 Ana a Bezai,+ 323. 18 Ana a Yora, 112. 19 Ana a Hasumu,+ 223. 20 Ana a Gibara,+ 95. 21 Ana a Betelehemu,+ 123. 22 Amuna a ku Netofa,+ 56. 23 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24 Ana a Azimaveti,+ 42. 25 Ana a Kiriyati-yearimu,+ Kefira ndi Beeroti, 743. 26 Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27 Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 28 Amuna a ku Beteli+ ndi a ku Ai,+ 223. 29 Ana a Nebo,+ 52. 30 Ana a Magabisi, 156. 31 Ana a Elamu+ wina, 1,254. 32 Ana a Harimu,+ 320. 33 Ana a Lodi,+ Hadidi+ ndi Ono,+ 725. 34 Ana a Yeriko,+ 345. 35 Ana a Senaya,+ 3,630.

36 Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a m’nyumba ya Yesuwa,+ 973. 37 Ana a Imeri,+ 1,052. 38 Ana a Pasuri,+ 1,247. 39 Ana a Harimu,+ 1,017.

40 Alevi:+ Ana a Yesuwa,+ a m’nyumba ya Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya,+ 74. 41 Oimba, ana a Asafu,+ 128. 42 Ana a alonda a pachipata, omwe anali ana a Salumu,+ ana a Ateri,+ ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita,+ ndi ana a Sobai, onse analipo 139.

43 Anetini:+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,+ 44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni,+ 45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46 ana a Hagabu, ana a Salimai,+ ana a Hanani, 47 ana a Gideli, ana a Gahara,+ ana a Reyaya, 48 ana a Rezini,+ ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49 ana a Uziza, ana a Paseya,+ ana a Besai, 50 ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu,+ 51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,+ 52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,+ 53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,+ 54 ana a Neziya, ana a Hatifa.+

55 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,+ 57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu, ana a Ami.+

58 Anetini+ onse pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.+

59 Ndiyeno amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ndipo sanathe kupereka umboni wotsimikizira kumene anachokera komanso kuti makolo awo+ anali Aisiraeli, ndi awa: 60 ana a Delaya, ana a Tobia, ndi ana a Nekoda,+ 652. 61 Ana a ansembe+ anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai+ amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ Mgiliyadi n’kuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62 Amenewa ndiwo anayang’ana mayina awo m’kaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Zitatero anawaletsa kuti asatumikire monga ansembe chifukwa anali oipitsidwa.+ 63 Pa chifukwa chimenechi, Tirisata*+ anawauza kuti sayenera kudya+ zinthu zopatulika koposa, kufikira patakhala wansembe wokhala ndi Urimu+ ndi Tumimu.

64 Mpingo wonsewo monga gulu limodzi+ unali ndi anthu 42,360,+ 65 kupatulapo akapolo awo aamuna ndi akapolo awo aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna+ ndi aakazi 200. 66 Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245.+ 67 Ngamila zawo zinalipo 435. Abulu awo analipo 6,720.+

68 Atsogoleri ena+ a nyumba za makolo awo+ atafika kunyumba ya Yehova+ imene inali ku Yerusalemu,+ anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwe pamalo ake.+ 69 Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka golide+ kuti athandize pa ntchitoyo wokwana madalakima* 61,000, siliva+ wokwana ma mina* 5,000 ndi mikanjo 100+ ya ansembe. 70 Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena,+ oimba, alonda a pazipata, Anetini ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala m’mizinda yawo.+

3 Pofika mwezi wa 7,+ ana a Isiraeli anali akukhala m’mizinda yawo. Ndiyeno anthuwo anayamba kusonkhana ku Yerusalemu+ monga munthu mmodzi.+ 2 Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi abale ake ansembe, ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, ananyamuka n’kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa+ m’chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu woona.

3 Chotero iwo anamanga guwa lansembe lolimba pamalo ake+ akale, chifukwa anali kuopa anthu a mitundu ina.+ Atatero anayamba kuperekerapo nsembe zopsereza kwa Yehova, zam’mawa ndi zamadzulo.+ 4 Kenako iwo anachita chikondwerero cha misasa+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+ Pachikondwererochi, anthuwo anali kubweretsa nsembe zopsereza paguwa lansembe tsiku ndi tsiku, mogwirizana ndi lamulo la nsembe zimene zinayenera kuperekedwa tsiku lililonse.+ 5 Ndiyeno anayamba kupereka nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ nsembe ya masiku okhala mwezi,+ ndi nsembe za panyengo zonse zochita zikondwerero zopatulika+ za Yehova. Analinso kupereka nsembe za aliyense amene anapereka chopereka chaufulu+ kwa Yehova ndi mtima wonse. 6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 7+ kupita m’tsogolo, anthuwo anayamba kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Pa nthawiyi n’kuti maziko a kachisi wa Yehova asanamangidwe.

7 Kenako anthuwo anapereka ndalama+ kwa anthu osema miyala+ ndi kwa amisiri,+ ndiponso anapereka chakudya,+ zakumwa ndi mafuta+ kwa Asidoni+ ndi kwa anthu a ku Turo,+ kuti abweretse matabwa a mkungudza kuchokera ku Lebanoni+ n’kudzawasiya m’mphepete mwa nyanja ku Yopa.+ Anachita zimenezi malinga ndi chilolezo chimene Koresi+ mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.

8 M’chaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, m’mwezi wachiwiri,+ Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi, ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchitoyo. Kenako anaika Alevi+ m’malo awo kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo kuti akhale oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova.+ 9 Chotero Yesuwa,+ ana ake ndi abale ake, Kadimiyeli ndi ana ake, ndi ana a Yuda,* ananyamuka monga gulu limodzi kukayang’anira anthu ogwira ntchito m’nyumba ya Mulungu woona. Komanso panali ana a Henadadi,+ ana awo ndi abale awo, omwe anali Alevi.

10 Tsopano anthu amene anali kugwira ntchito yomanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko+ a kachisi wa Yehova. Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe+ omwe ananyamula malipenga,+ ndiponso Alevi ana a Asafu+ omwe ananyamula zinganga,+ anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo+ limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa. 11 Iwo anayamba kuimba molandizana potamanda+ ndi kuthokoza Yehova kuti, “iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kosatha kumene amakusonyeza kwa Isiraeli kudzakhala mpaka kalekale.”*+ Ndipo anthu onse anafuula mokweza kwambiri+ potamanda Yehova chifukwa cha kumangidwa kwa maziko a nyumba ya Yehova. 12 Ansembe+ ndi Alevi ambiri, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ amuna okalamba amene anaona nyumba yoyambirira,+ anali kulira+ mokweza chifukwa cha kumangidwa kwa maziko+ a nyumbayo pamaso pawo, ndipo enanso ambiri anali kufuula mosangalala.+ 13 Chotero anthu sanathe kusiyanitsa phokoso lawo losonyeza kusangalala+ ndi losonyeza kulira, chifukwa anthuwo anali kufuula kwambiri, ndipo phokoso lawo linali kumveka kutali kwambiri.

4 Adani+ a Yuda ndi Benjamini atamva kuti anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo+ akumangira kachisi Yehova Mulungu wa Isiraeli, 2 nthawi yomweyo anapita kwa Zerubabele+ ndi kwa atsogoleri+ a nyumba za makolo n’kukawauza kuti: “Bwanji timangire nanu limodzi,+ popeza ifeyo mofanana ndi inuyo, timapembedza Mulungu wanu+ ndipo timapereka nsembe kwa iye, kuyambira m’masiku a Esari-hadoni+ mfumu ya Asuri, yemwe anatibweretsa kuno.”+ 3 Koma Zerubabele, Yesuwa,+ ndi atsogoleri ena onse+ a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Mulibe ufulu womanga nafe limodzi nyumba ya Mulungu wathu,+ pakuti ifeyo patokha timangira limodzi nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga momwe Mfumu Koresi+ ya Perisiya yatilamulira.”

4 Kuyambira pamenepo, anthu a m’dzikolo anakhala akufooketsa+ manja a anthu a ku Yuda ndi kuwagwetsa ulesi pa ntchito yomanga.+ 5 Komanso, anali kulemba ntchito+ aphungu kuti alepheretse zolinga zawo masiku onse a Koresi mfumu ya Perisiya, mpaka ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya. 6 Mu ulamuliro wa Ahasiwero, kumayambiriro kwa ulamuliro wake, iwo analemba kalata yoneneza+ anthu okhala ku Yuda ndi ku Yerusalemu. 7 Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzake ena onse analemba kalata kwa Aritasasita mfumu ya Perisiya m’masiku a mfumuyo. Kalatayo anaimasulira m’Chiaramu n’kuilemba m’zilembo za Chiaramu.+

8 Rehumu mtsogoleri wa akulu a boma ndi Simusai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Aritasasita yotsutsana ndi Yerusalemu, kuti: 9 Kuchokera kwa Rehumu+ mtsogoleri wa akulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse monga oweruza ndi abwanamkubwa aang’ono a kutsidya lina la Mtsinje,*+ alembi+ ena, anthu a ku Ereke,+ Ababulo,+ anthu okhala ku Susa,+ kapena kuti Aelamu,+ 10 mitundu ina yonse+ imene Asinapera+ wamkulu ndi wolemekezeka anaitenga ukapolo n’kukaiika m’mizinda ya ku Samariya,+ ndi ena onse a kutsidya lina la Mtsinje . . . Tsopano 11 izi n’zimene analemba m’kalata imene anatumizayo:

“Kwa mfumu Aritasasita,+ kuchokera kwa ife akapolo anu, amuna a kutsidya lina la Mtsinje: Tsopano 12 inu mfumu dziwani kuti Ayuda amene anachokera kwa inu n’kudzatipeza kuno, ali ku Yerusalemu. Iwo akumanga mzinda woukira ndi woipa uja, ndipo akumanga mpanda+ ndi kukonzanso maziko ake. 13 Ndiyeno inu mfumu dziwani kuti, mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake n’kumalizidwa, anthu amenewa asiya kupereka msonkho umene munthu aliyense amapereka,+ msonkho wakatundu,+ ndi msonkho wapanjira ndipo zimenezi zidzachititsa kuti chuma+ cha mafumu chiwonongeke. 14 Tsopano popeza ife timalandira malipiro ochokera kunyumba yachifumu,* si bwino kuti tingolekerera kuti inu mfumu chuma chanu chiwonongeke. Pa chifukwa chimenechi, tatumiza kalatayi kuti tikudziwitseni zimenezi inu mfumu 15 n’cholinga choti mufufuze m’buku la mbiri+ ya makolo anu. Mukafufuza m’bukulo mupeza kuti mzinda umenewu ndi mzinda woukira ndi wowonongetsa chuma cha mafumu ndi zigawo za mayiko. Mupezanso kuti mumzinda umenewu mwakhala muli anthu oyambitsa kupanduka kuyambira kalekale. N’chifukwa chake mzindawu uli bwinja.+ 16 Tikukudziwitsani mfumu kuti mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake n’kumalizidwa, ndithu simudzakhala ndi gawo kutsidya lino la Mtsinje.”+

17 Ndiyeno mfumuyo inatumiza mawu kwa Rehumu+ mtsogoleri wa akulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse+ amene anali kukhala ku Samariya, ndi kwa ena onse okhala kutsidya lina la Mtsinje. Mawuwo anali akuti:

“Moni!+ 18 Kalata imene mwatitumizira aiwerenga momveka bwino pamaso panga. 19 Choncho ine ndinalamula kuti afufuze, ndipo atafufuza+ apeza kuti mzinda umenewo kuyambira kale wakhala ukuukira mafumu, ndiponso anthu a mumzindawo akhala akupanduka ndi kugalukira.+ 20 Panali mafumu amphamvu+ olamulira Yerusalemu ndi dera lonse la kutsidya lina la Mtsinje+ ndipo anali kupatsidwa msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu, ndi msonkho wapanjira.+ 21 Tsopano ikani lamulo loti amuna amenewa asiye ntchitoyo, ndi kuti mzinda umenewo usamangidwenso kufikira ine ndikadzalamula. 22 Muonetsetse kuti musanyalanyaze kuchita zimenezi kuti vuto limeneli lingakule, zomwe zingapweteketse mafumu.”+

23 Mawu amene analembedwa m’kalata ya mfumu Aritasasita atawerengedwa pamaso pa Rehumu,+ Simusai+ mlembi, ndi anzawo,+ iwo anapita msangamsanga kwa Ayuda ku Yerusalemu n’kukawaletsa ntchitoyo mwankhondo.+ 24 Panali pa nthawi imeneyi pamene ntchito yomanga nyumba ya Mulungu, imene inali ku Yerusalemu, inaima ndipo inakhala chiimire mpaka chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya.

5 Mneneri Hagai+ ndi mneneri Zekariya+ mdzukulu wa Ido,+ analosera kwa Ayuda amene anali mu Yuda ndi mu Yerusalemu, m’dzina+ la Mulungu wa Isiraeli yemwe anali nawo.+ 2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza. 3 Pa nthawi imeneyo Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai, ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo n’kudzawafunsa kuti: “Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi ndi kumaliza khoma* lamatabwali?”+ 4 Anawafunsanso kuti: “Amuna amene akumanga nyumba imeneyi mayina awo ndani?” 5 Koma maso+ a Mulungu wawo anali+ pa akulu a Ayuda, ndipo anthu aja sanawasiyitse ntchitoyo. Anadikira mpaka pamene analemba chikalata chokhudza nkhaniyo n’kuchitumiza kwa Dariyo, ndiponso mpaka pamene chikalata choyankha nkhani imeneyi chinabwera.

6 Izi n’zimene zinali m’kalata+ imene Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,+ Setara-bozenai+ ndi anzake,+ ndiponso abwanamkubwa aang’ono amene anali kutsidya lina la Mtsinje, anatumiza kwa mfumu Dariyo. 7 Anatumiza mawu kwa iye, ndipo kalatayo anailemba motere:

“Kwa Mfumu Dariyo:

“Mtendere ukhale nanu.+ 8 Inu mfumu dziwani kuti ife tinapita kuchigawo+ cha Yuda kunyumba ya Mulungu wamkulu.+ Kumeneko takapeza kuti nyumbayo akuimanga ndi miyala yochita kuigubuduzira pamalo ake ndiponso akuika matabwa m’makoma ake. Iwo akugwira ntchitoyo mwakhama ndipo ikupita patsogolo. 9 Ndiyeno ife tinafunsa akuluakulu amenewo kuti: ‘Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi ndi kumaliza khoma lamatabwali?’+ 10 Tinawafunsanso mayina awo kuti tilembe mayina a atsogoleri awo, n’cholinga choti tikuuzeni kuti muwadziwe.+

11 “Akuluakuluwo anatiyankha kuti: ‘Ife ndife atumiki a Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi,+ ndipo tikumanganso nyumba imene inamangidwa zaka zambiri zapitazo, imene mfumu yaikulu ya Isiraeli inamanga ndi kuimaliza.+ 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa+ Mulungu wakumwamba, iye anawapereka+ m’manja mwa Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo Mkasidi,+ yemwe anagwetsa nyumbayi+ n’kutengera anthuwo ku ukapolo ku Babulo.+ 13 Komabe m’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Babulo, mfumu Koresi inaika lamulo loti nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.+ 14 Komanso, ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara anazitenga m’kachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, n’kupita nazo kukachisi wa ku Babulo,+ mfumu Koresi+ inazichotsa m’kachisi wa ku Babuloyo. Ndiyeno zinaperekedwa kwa Sezibazara,+ munthu amene Koresi anamuika kukhala bwanamkubwa.+ 15 Koresiyo anamuuza iye kuti: “Tenga ziwiya izi.+ Pita ukaziike m’kachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo ukaonetsetse kuti nyumba ya Mulungu yamangidwanso pamalo ake.”+ 16 Sezibazarayo atabwera anamanga maziko a nyumba ya Mulungu+ yomwe ili ku Yerusalemu. Kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano nyumbayi ikumangidwanso ndipo sinamalizidwe.’+

17 “Tsopano ngati inu mfumu mukuona kuti n’koyenera, uzani anthu afufuze+ m’nyumba ya chuma cha mfumu imene ili ku Babuloko, kuti aone ngati mfumu Koresi inaikadi lamulo+ loti nyumba ya Mulungu yomwe ili ku Yerusalemu imangidwenso. Inu mfumu mutitumizire chigamulo chanu pankhani imeneyi.”

6 Panali pa nthawi imeneyi pamene mfumu Dariyo inaika lamulo loti afufuze ndipo anafufuza m’nyumba yosungiramo mabuku ofotokoza mbiri yakale,+ momwe analinso kusungiramo zinthu zamtengo wapatali zimene zinaikidwa ku Babuloko. 2 Ku malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri a ku Ekibatana, m’chigawo cha dziko la Amedi,+ anapezako mpukutu. Mumpukutuwo munalembedwa uthenga wakuti:

3 “M’chaka choyamba cha Mfumu Koresi,+ mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti: Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe+ kumeneko, ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo kutalika kwake kuchokera pansi kufika pamwamba ikhale mikono* 60, ndiponso m’lifupi mwake ikhale mikono 60.+ 4 Ikhale ndi mizere itatu ya miyala yochita kuigubuduzira+ pamalopo ndi mzere umodzi wa matabwa.+ Ndalama zake zichokere kunyumba ya mfumu.+ 5 Komanso ziwiya zagolide ndi zasiliva+ za m’nyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara+ anazichotsa m’kachisi yemwe anali ku Yerusalemu n’kuzipititsa ku Babulo, zibwezedwe kuti zipite kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe m’nyumba ya Mulungu.+

6 “Tsopano inu Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai+ ndi anzanu ndiponso abwanamkubwa aang’ono+ amene ali kutsidya lina la Mtsinje, musakasokoneze kumeneko.+ 7 Musakalowerere ntchito yomanga nyumba ya Mulunguyo.+ Bwanamkubwa wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amanganso nyumba ya Mulunguyo pamalo ake. 8 Ineyo ndaika lamulo+ lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa+ ndalama mosalekeza+ zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho. 9 Komanso muziwapatsa zinthu zofunika monga ng’ombe zing’onozing’ono zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ndi ana a nkhosa+ kuti azipereka nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba. Muziwapatsanso tirigu,+ mchere,+ vinyo+ ndi mafuta+ monga mmene anganenere ansembe amene ali ku Yerusalemu. Musalephere kuwapatsa zinthu zimenezi tsiku ndi tsiku mosalekeza. 10 Muziwapatsa zimenezi kuti nthawi zonse+ azipereka nsembe zoziziritsa mtima+ kwa Mulungu wakumwamba, ndiponso kuti azipempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.+ 11 Ndaikanso lamulo lakuti aliyense wophwanya+ lamulo limeneli, thabwa+ lidzazulidwa panyumba yake ndipo iye adzapachikidwa+ pathabwalo. Komanso nyumba yake idzasandutsidwa chimbudzi cha aliyense chifukwa cha zimenezi.+ 12 Mulungu amene anaika dzina lake+ kumeneko, achotse mfumu iliyonse ndi anthu alionse ophwanya lamulo limeneli ndiponso owononga+ nyumba ya Mulungu imene ili ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndaika lamulo limeneli, ndipo zichitike mwamsanga.”

13 Kenako Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,+ Setara-bozenai+ ndi anzawo anachita mogwirizana ndi mawu amene mfumu Dariyo inatumiza. Anachita zimenezi mwamsanga. 14 Tsopano akulu+ a Ayuda anali kupita patsogolo pa ntchito yomanga+ nyumbayo atalimbikitsidwa ndi ulosi wa mneneri Hagai+ ndi Zekariya+ mdzukulu wa Ido.+ Iwo anamanga nyumbayo ndi kuimaliza potsatira lamulo la Mulungu wa Isiraeli,+ ndi lamulo la Koresi,+ Dariyo,+ ndi Aritasasita+ mfumu ya Perisiya. 15 Iwo anali atamaliza kumanga nyumbayo pofika tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,+ m’chaka cha 6 cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.

16 Ndiyeno ana a Isiraeli, ansembe, Alevi+ ndi anthu ena onse amene anachokera ku ukapolo,+ anatsegulira+ nyumba ya Mulunguyo mosangalala. 17 Pamwambo wotsegulira nyumba ya Mulunguyo, anapereka nsembe ng’ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, ndi ana a nkhosa amphongo 400. Anaperekanso mbuzi zamphongo 12 za nsembe ya machimo ya ana onse a Isiraeli mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Isiraeli.+ 18 Kenako anaika ansembe ndi Alevi m’magulu awo+ kuti azichita utumiki wa Mulungu ku Yerusalemu, mogwirizana ndi malangizo a m’buku la Mose.+

19 Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita pasika+ pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.+ 20 Chifukwa chakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ monga gulu limodzi, onse anali oyera. Choncho Aleviwo anapha nyama ya pasika+ ya anthu onse amene anachokera ku ukapolo, ya abale awo ansembe, ndiponso yawo. 21 Ndiyeno ana a Isiraeli amene anabwera kuchokera ku ukapolo anadya+ nyamayo. Komanso aliyense amene anadzilekanitsa ku zonyansa+ za anthu a mitundu ina ya m’dzikolo n’kubwera kwa iwo ndi kufunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anadya nawo.+ 22 Kwa masiku 7, iwo anachita mosangalala chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pakuti Yehova anawachititsa kusangalala. Iye anatembenuzira+ kwa iwo mtima wa mfumu ya Asuri kuti ilimbitse manja awo pa ntchito yomanga nyumba ya Mulungu woona, Mulungu wa Isiraeli.

7 Pambuyo pa zimenezi, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, panali mwamuna wina dzina lake Ezara.+ Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+ 2 Hilikiya anali mwana wa Salumu,+ Salumu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Ahitubu,+ 3 Ahitubu anali mwana wa Amariya,+ Amariya anali mwana wa Azariya,+ Azariya anali mwana wa Merayoti,+ 4 Merayoti anali mwana wa Zerahiya,+ Zerahiya anali mwana wa Uzi,+ Uzi anali mwana wa Buki,+ 5 Buki anali mwana wa Abisuwa,+ Abisuwa anali mwana wa Pinihasi,+ Pinihasi anali mwana wa Eleazara,+ ndipo Eleazara anali mwana wa Aroni+ wansembe wamkulu.+ 6 Ezara ameneyu ananyamuka n’kuchoka ku Babulo. Iye anali katswiri wodziwa kukopera+ chilamulo cha Mose,+ chimene Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka. Chotero mfumu inamupatsa zopempha zake zonse chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.+

7 Choncho ena mwa ana a Isiraeli, ansembe,+ Alevi,+ oimba,+ alonda a pazipata,+ ndi Anetini+ anapita ku Yerusalemu m’chaka cha 7 cha mfumu Aritasasita.+ 8 Patapita nthawi, Ezara anafika ku Yerusalemu m’mwezi wachisanu, m’chaka cha 7 cha mfumuyo. 9 Zinatero chifukwa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, iye analamula anthu kuti anyamuke ku Babulo, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, iye anafika ku Yerusalemu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye,+ 10 popeza Ezara anakonza+ mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova+ ndi kuchichita+ ndiponso kuti aphunzitse+ mu Isiraeli malamulo+ ndi chilungamo.+

11 Izi n’zimene zinali m’kalata imene Mfumu Aritasasita inapatsa wansembe Ezara wokopera zinthu, wokopera+ mawu a malamulo a Yehova ndi malangizo ake kwa Aisiraeli:

12 “Kuchokera kwa Aritasasita,+ mfumu ya mafumu,+ kupita kwa wansembe Ezara, wokopera chilamulo cha Mulungu wakumwamba:+ Ukhale ndi mtendere wochuluka.+ Tsopano 13 ine ndaika lamulo+ lakuti aliyense mu ufumu wanga+ pakati pa anthu a Isiraeli, ansembe awo, ndi Alevi amene akufuna kupita nawe ku Yerusalemu apite.+ 14 Popeza kuchokera kwa mfumu ndi aphungu ake 7+ lamulo linaperekedwa kuti afufuze+ zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, m’chilamulo+ cha Mulungu+ wako chimene chili m’manja mwako, 15 ndi kutinso munyamule siliva ndi golide zimene mfumu ndi aphungu ake apereka mwaufulu+ kwa Mulungu wa Isiraeli, amene amakhala ku Yerusalemu.+ 16 Munyamulenso siliva ndi golide yense amene mum’peze m’chigawo chonse cha Babulo, limodzi ndi mphatso za anthu+ ndi za ansembe omwe akupereka mwaufulu kunyumba ya Mulungu wawo,+ yomwe ili ku Yerusalemu. 17 Ndi ndalama zimenezi, ukagule mwamsangamsanga ng’ombe zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ana a nkhosa amphongo,+ limodzi ndi nsembe zake zambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ Zimenezi ukazipereke paguwa lansembe la panyumba ya Mulungu wako,+ yomwe ili ku Yerusalemu.+

18 “Zilizonse zimene iweyo ndi abale ako mudzaone kuti n’zabwino kuchita ndi siliva ndi golide wotsalayo,+ mogwirizana ndi chifuniro+ cha Mulungu wanu, mudzachite zimenezo.+ 19 Ziwiya+ zimene ukupatsidwa kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wako, ukazipereke zonse ku Yerusalemu n’kukaziika pamaso pa Mulungu.+ 20 Zinthu zina zonse zofunika panyumba ya Mulungu wako zimene ukuyenera kupereka, udzazitenge kunyumba ya mfumu yosungiramo chuma.+

21 “Ineyo mfumu Aritasasita ndalamula+ asungichuma onse+ amene ali kutsidya lina la Mtsinje,*+ kuti chilichonse chimene wansembe Ezara,+ wokopera chilamulo cha Mulungu wakumwamba, angapemphe kwa inu chichitidwe mwamsanga. 22 Mum’patse ngakhale matalente* 100+ a siliva, tirigu wokwana miyezo 100 ya kori,*+ vinyo+ wokwana mitsuko*+ 100, mafuta okwana mitsuko 100,+ ndi mchere+ wochuluka. 23 Zonse zimene Mulungu wakumwamba+ walamula+ zokhudza nyumba yake, zichitike modzipereka kwambiri+ kuti mkwiyo usayakire dziko la mfumu ndiponso usayakire ana ake.+ 24 Amuna inu mudziwe kuti ansembe,+ Alevi,+ oimba,+ alonda a pakhomo,+ Anetini,+ ndi anthu ogwira ntchito panyumba ya Mulunguyi, musawakhometse msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu,+ kapena msonkho wapanjira.+

25 “Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru+ zimene Mulungu wako wakupatsa, uike anthu osungitsa malamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza+ anthu onse a kutsidya lina la Mtsinje, ngakhalenso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense wosadziwa malamulowo, amuna inu mum’phunzitse.+ 26 Aliyense wosatsatira chilamulo cha Mulungu wako+ ndi chilamulo cha mfumu, azipatsidwa chiweruzo msangamsanga, kaya choti aphedwe,+ athamangitsidwe,+ alipitsidwe ndalama,+ kapena aikidwe m’ndende.”

27 Atamandike Yehova Mulungu wa makolo athu,+ amene waika maganizo amenewa mumtima+ mwa mfumu, kuti nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu ikongoletsedwe.+ 28 Iye wandisonyeza kukoma mtima kosatha+ pamaso pa mfumu, pamaso pa aphungu ake,+ ndi pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinadzilimbitsa chifukwa dzanja+ la Yehova Mulungu wanga linali pa ine, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti apite nane limodzi.

8 Tsopano nawa mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo+ a anthu amene anachoka nane ku Babulo, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita:+ 2 Pa ana a Pinihasi+ panali Gerisomu, pa ana a Itamara+ panali Danieli,+ pa ana a Davide+ panali Hatusi. 3 Panalinso Zekariya kuchokera pa ana a Sekaniya, yemwe anali wochokera pa ana a Parosi.+ Iye anali ndi amuna amene analembetsa mayina awo okwanira 150. 4 Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Eliho-enai mwana wa Zerahiya. Iye anali ndi amuna 200. 5 Pa ana a Zatu+ panali Sekaniya mwana wa Yahazieli. Iye anali ndi amuna 300. 6 Pa ana a Adini+ panali Ebedi mwana wa Yonatani. Iye anali ndi amuna 50. 7 Pa ana a Elamu+ panali Yesaiya mwana wa Ataliya. Iye anali ndi amuna 70. 8 Pa ana a Sefatiya+ panali Zebadiya mwana wa Mikayeli. Iye anali ndi amuna 80. 9 Pa ana a Yowabu panali Obadiya mwana wa Yehiela. Iye anali ndi amuna 218. 10 Pa ana a Bani+ panali Selomiti mwana wa Yosifiya. Iye anali ndi amuna 160. 11 Pa ana a Bebai+ panali Zekariya mwana wa Bebai. Iye anali ndi amuna 28. 12 Pa ana a Azigadi+ panali Yohanani mwana wa Hakatani. Iye anali ndi amuna 110. 13 Anthu ochokera pa ana a Adonikamu+ omwe anali omaliza, mayina awo anali awa: Elifeleti, Yeyeli ndi Semaya. Iwo anali ndi amuna 60. 14 Pa ana a Bigivai+ panali Utai ndi Zabudi. Iwo anali ndi amuna 70.

15 Ndiyeno ndinawasonkhanitsa pamtsinje+ umene umafika ku Ahava+ ndipo tinamanga msasa pamenepo n’kukhalapo masiku atatu kuti ndiwaonetsetse anthuwo+ ndi ansembe,+ koma sindinapezepo ana a Levi.+ 16 Choncho ndinaitanitsa Eliezere, Ariyeli, Semaya, Elinatani, Yaribi, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu. Amenewa anali atsogoleri awo. Ndinaitanitsanso Yoyaribi ndi Elinatani, omwe anali alangizi.+ 17 Kenako ndinawalamula kuti apite kwa Ido yemwe anali mtsogoleri pamalo otchedwa Kasifiya. Ndinawauza mawu+ oti akauze Ido ndi abale ake Anetini+ ku Kasifiyako, kuti atibweretsere atumiki+ a panyumba ya Mulungu wathu. 18 Chotero, popeza dzanja labwino+ la Mulungu wathu linali pa ife, iwo anatibweretsera munthu wanzeru+ wochokera pakati pa ana a Mali+ mdzukulu wa Levi+ mwana wa Isiraeli, dzina lake Serebiya+ pamodzi ndi ana ake ndi abale ake. Onse pamodzi analipo 18. 19 Panalinso Hasabiya, yemwe anali pamodzi ndi Yesaiya wochokera pa ana a Merari,+ abale ake ndi ana awo. Onse pamodzi analipo 20. 20 Kuchokera pa Anetini amene Davide ndi akalonga anawaika kuti azitumikira Alevi, panali Anetini 220. Onsewa anawasankha pochita kuwatchula mayina awo.

21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava kuja, kuti tidzichepetse+ pamaso pa Mulungu wathu ndi kumupempha kuti atisonyeze njira yoyenera+ kwa ife, ana athu,+ ndi katundu wathu yense. 22 Ndinatero pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu lankhondo+ ndi okwera pamahatchi+ kuti atithandize kumenyana ndi adani m’njira, chifukwa tinali titauza mfumuyo kuti: “Dzanja+ la Mulungu wathu lili ndi onse om’funafuna kuti awachitire zabwino,+ koma mkwiyo wake+ wamphamvu umayakira onse omusiya.”+ 23 Chotero tinasala kudya+ n’kupempha+ Mulungu wathu zimenezi, moti iye anamva pempho+ lathu.

24 Tsopano ndinapatula anthu 12 kuchokera pa atsogoleri a ansembe. Mayina awo anali Serebiya+ ndi Hasabiya+ pamodzi ndi abale awo 10. 25 Ndiyeno ndinawayezera siliva, golide ndi ziwiya.+ Zimenezi zinali zopereka za kunyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu,+ aphungu ake,+ akalonga ake ndi Aisiraeli onse+ amene anali kumeneko anapereka. 26 Chotero ndinawayezera n’kuwapatsa siliva wokwana matalente* 650, ziwiya 100 zasiliva+ zokwana matalente awiri, golide wokwana matalente 100, 27 mbale 20 zing’onozing’ono zagolide zolowa zokwana madariki* 1,000 ndi ziwiya ziwiri zamkuwa wabwino wonyezimira mofiirira, zamtengo wapatali ngati golide.

28 Kenako ndinawauza kuti: “Inu ndinu oyera+ kwa Yehova. Ziwiyazi+ ndi zopatulika ndipo siliva ndi golideyu ndi nsembe yaufulu yopita kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. 29 Khalani maso ndipo khalani atcheru mpaka mukaziyeze+ pamaso pa atsogoleri a ansembe, atsogoleri a Alevi ndi pamaso pa akalonga a makolo a Aisiraeli ku Yerusalemu, m’zipinda zodyera+ za panyumba ya Yehova.” 30 Ansembe ndi Aleviwo analandira siliva ndi golide amene anayezedwayo ndiponso ziwiya zimene zinayezedwazo, kuti apititse zinthuzi ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.+

31 Pomalizira pake tinachoka pamtsinje wa Ahava+ pa tsiku la 12 la mwezi woyamba+ kuti tipite ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu wathu linali nafe pa ulendowu moti anatipulumutsa+ m’manja mwa adani ndiponso kwa achifwamba a m’njira. 32 Kenako tinafika ku Yerusalemu+ n’kukhala kumeneko masiku atatu. 33 Pa tsiku lachinayi tinayeza siliva, golide+ ndi ziwiya+ zija m’nyumba ya Mulungu wathu. Titatero tinapereka zinthuzo m’manja mwa wansembe Meremoti+ mwana wa Uliya, yemwe anali limodzi ndi Eleazara mwana wa Pinihasi. Iwowa anali limodzi ndi Yozabadi+ mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binui,+ omwe anali Alevi. 34 Zinthu zonsezo tinaziwerenga n’kuziyeza kenako tinalemba kulemera kwa zinthu zonsezo pa nthawiyo. 35 Anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo,+ amene kale anali m’dziko la eni, anapereka nsembe zopsereza+ kwa Mulungu wa Isiraeli. Anapereka ng’ombe zamphongo 12+ za Aisiraeli onse, nkhosa zamphongo 96,+ ana a nkhosa amphongo 77, ndi mbuzi zamphongo 12+ monga nsembe yamachimo. Zonsezi anazipereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova.

36 Kenako tinapereka malamulo+ a mfumu kwa masatarapi*+ a mfumu ndi abwanamkubwa+ a kutsidya lina la Mtsinje.*+ Iwo anathandiza anthuwo+ ndiponso anathandiza panyumba ya Mulungu woona.

9 Zinthu zimenezi zitangotha, akalonga+ anabwera kwa ine n’kundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule+ kwa anthu a mitundu ina pa nkhani ya zinthu zonyansa+ za anthu a mitundu inawo. Anthu ake ndi Akanani,+ Ahiti,+ Aperezi,+ Ayebusi,+ Aamoni,+ Amowabu,+ Aiguputo+ ndi Aamori.+ 2 Iwo alola ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna,+ ndipo iwo omwe ndi mtundu wopatulika,+ asakanikirana+ ndi anthu a mitundu ina. Akalonga ndi atsogoleri ndiwo ali patsogolo+ pa kusakhulupirika kumeneku.”

3 Nditangomva nkhani imeneyi, ndinang’amba zovala zanga+ n’kuyamba kuzula tsitsi la m’mutu mwanga+ ndi ndevu zanga, ndipo ndinakhala pansi ndili wokhumudwa ndi wachisoni kwambiri.+ 4 Iwo anayamba kusonkhana kwa ine, aliyense akunjenjemera+ chifukwa cha mawu a Mulungu wa Isiraeli otsutsa kusakhulupirika kwa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo. Pa nthawiyi n’kuti ine nditakhala pansi ndili wokhumudwa ndi wachisoni kwambiri, ndipo ndinakhala choncho mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo.+

5 Pa nthawi yopereka nsembe yambewu+ yamadzulo, pambuyo podzichepetsa mwanjira imeneyi, ndinaimirira, zovala zanga zitang’ambika, ndipo ndinagwada+ n’kutambasulira manja anga kwa Yehova Mulungu wanga.+ 6 Kenako ndinayamba kunena kuti:+ “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi+ kuti ndikweze nkhope yanga kwa inuyo Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu+ zachuluka pamutu pathu ndipo machimo athu achuluka kwambiri mpaka kufika kumwamba.+ 7 Kuyambira masiku a makolo athu+ mpaka lero, takhala m’machimo aakulu kwambiri,+ ndipo chifukwa cha zolakwa zathu, ifeyo, mafumu athu,+ ndi ansembe athu,+ taperekedwa m’manja mwa mafumu a mayiko ena ndi lupanga,+ mwa kutengedwa ukapolo,+ kulandidwa katundu,+ komanso kukhala ndi nkhope zamanyazi+ ngati mmene tilili lero. 8 Tsopano kwa nthawi yochepa, Yehova Mulungu wathu watikomera mtima+ mwa kutisiyira anthu opulumuka,+ ndiponso mwa kutipatsa malo otetezeka* m’malo ake oyera kuti maso athu awale,+ inu Mulungu wathu, ndi kutitsitsimutsa pang’ono mu ukapolo wathu.+ 9 Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo,+ koma watisonyeza kukoma mtima kosatha pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse n’cholinga choti tikamange nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anali bwinja,+ ndi kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.+

10 “Ndiye tinganene chiyani inu Mulungu wathu pambuyo pa zimene zachitikazi? Popeza tasiya malamulo anu+ 11 amene munatilamula kudzera mwa atumiki anu aneneri, akuti, ‘Dziko limene anthu inu mukukalitenga kukhala lanu ndi lodetsedwa chifukwa cha kudetsedwa kwa anthu a mitundu ina,+ ndiponso chifukwa cha zonyansa zawo+ zimene adzaza nazo dzikolo. Iwo adzaza dzikolo ndi zodetsa kuyambira koyambirira mpaka kumapeto.+ 12 Choncho musakapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna,+ kapena kutenga ana awo aakazi n’kuwapereka kwa ana anu aamuna. Ndipo mpaka kalekale, musakawathandize kukhala ndi mtendere+ ndiponso kutukuka. Mukachite zimenezi kuti mukakhale amphamvu+ ndiponso kuti mukadyedi zabwino za dzikolo ndi kulitengadi kuti likhale la ana anu mpaka kalekale.’+ 13 Tsopano pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha zochita zathu zoipa+ ndi machimo athu ochuluka, ngakhale kuti inuyo Mulungu wathu simunatilange monga mmene tinafunika kulangidwira+ ndipo mwalola kuti anthu onsewa apulumuke,+ 14 kodi zoona tiphwanyenso malamulo anu kachiwiri ndi kupanga mapangano a ukwati+ ndi anthu a mitundu ina ochita zonyansawa?+ Kodi tikatero simutikwiyira koopsa+ mwakuti sipakhalanso wotsala+ ndi wopulumuka? 15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+

10 Tsopano Ezara atangomaliza kupemphera+ ndi kuvomereza machimo,+ komwe ankachita akulira ndiponso ali chogona+ patsogolo pa nyumba+ ya Mulungu woona, Aisiraeli anasonkhana kwa iye. Iwo anali mpingo waukulu kwambiri, amuna, akazi ndi ana, ndipo anali atalira kwambiri. 2 Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu, chifukwa tinatenga akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Koma tsopano Aisiraeli ali ndi chiyembekezo+ pa nkhani imeneyi. 3 Tsopano tiyeni tichite pangano+ ndi Mulungu wathu, lakuti tisiya+ akazi onse amenewa ndi ana awo mogwirizana ndi lamulo la Yehova ndi la anthu amene akunjenjemera+ chifukwa cha lamulo+ la Mulungu wathu, kuti zinthu zichitike mogwirizana ndi lamulo.+ 4 Choncho iweyo nyamuka, chifukwa nkhaniyi ili m’manja mwako ndipo ife tili nawe. Limba mtima ndi kuchitapo kanthu.”

5 Pamenepo Ezara ananyamuka ndipo anauza atsogoleri a ansembe, a Alevi ndi a Aisiraeli onse kuti alumbire+ kuti achita mogwirizana ndi mawu amenewa. Choncho iwo analumbira. 6 Tsopano Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona n’kupita kuchipinda chodyera+ cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye mkate+ kapena kumwa madzi, chifukwa anali kumva chisoni+ ndi kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.

7 Kenako anauza anthu kuti alengeze mu Yuda ndi Yerusalemu yense kwa anthu onse amene anachokera ku ukapolo+ kuti asonkhane ku Yerusalemu, 8 ndi kuti aliyense amene sabwera+ potha masiku atatu mogwirizana ndi lamulo la akalonga+ ndi akulu, katundu wake yense alandidwa+ ndipo iyeyo achotsedwa+ pa khamu la anthu amene anachokera ku ukapolo. 9 Choncho amuna onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu m’masiku atatu, ndipo umu munali m’mwezi wa 9,+ pa tsiku la 20 la mweziwo. Anthu onsewo anakhala pabwalo la nyumba ya Mulungu woona, akunjenjemera poganizira nkhaniyo komanso chifukwa kunali kugwa mvula yamvumbi.+

10 Patapita nthawi wansembe Ezara anaimirira n’kuuza anthuwo kuti: “Inuyo mwachita zosakhulupirika chifukwa mwatenga akazi achilendo+ n’kuwonjezera pa machimo a Isiraeli.+ 11 Tsopano vomerezani+ machimo anu kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, ndipo chitani zomusangalatsa+ ndi kudzipatula kwa anthu a mitundu ina ndiponso kwa akazi achilendo.”+ 12 Pamenepo mpingo wonsewo unayankha ndi mawu okweza kuti: “Tichita ndendende mogwirizana ndi mawu anuwo.+ 13 Komabe, tilipo anthu ambiri ndipo ino ndi nyengo ya mvula yamvumbi, choncho n’zosatheka kuima panja. Komanso nkhani imeneyi sitenga tsiku limodzi kapena masiku awiri chifukwa tachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi. 14 Choncho aloleni akalonga+ athu kuti aimire mpingo wonse ndipo anthu onse a m’mizinda yathu amene atenga akazi achilendo, abwere pa nthawi zimene zikhazikitsidwe. Abwere limodzi ndi akulu a mzinda uliwonse ndi oweruza ake, mpaka titathetsa mkwiyo wa Mulungu wathu umene watiyakira pa nkhani imeneyi.”

15 (Koma Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yahazeya mwana wa Tikiva anatsutsa+ zimenezi, ndipo Mesulamu ndi Sabetai,+ omwe anali Alevi, anawathandiza.) 16 Anthu amene anachokera ku ukapolowo+ anatsatira dongosolo limenelo, ndipo wansembe Ezara ndi amuna onse amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ omwe anachita kuwatchula mayina awo, anachoka pakati pa anthuwo n’kukakhala pansi kuti afufuze nkhaniyo,+ kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 10.+ 17 Pomalizira pake, pofika pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, anamaliza kufufuza amuna onse amene anatenga akazi achilendo.+ 18 Iwo anapeza kuti ana ena a ansembe+ anatenga akazi achilendo. Kuchokera pa ana a Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki+ ndi abale ake, panali Maaseya, Eliezere, Yaribi ndi Gedaliya. 19 Koma iwo analonjeza mwa kugwirana chanza kuti asiya akazi awo ndi kuti popeza anali atachimwa,+ nkhosa yamphongo iperekedwa+ chifukwa cha tchimo lawolo.

20 Pa ana a Imeri+ panali Haneni ndi Zebadiya. 21 Pa ana a Harimu+ panali Maaseya, Eliya, Semaya, Yehiela ndi Uziya. 22 Pa ana a Pasuri+ panali Elioenai, Maaseya, Isimaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa. 23 Pa Alevi panali Yozabadi, Simeyi, Kelaya (kapena kuti Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliezere. 24 Pa oimba panali Eliyasibu. Pa alonda a pachipata panali Salumu, Telemu ndi Uri.

25 Kuchokera pa Aisiraeli, pa ana a Parosi+ panali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eleazara, Malikiya ndi Benaya. 26 Pa ana a Elamu+ panali Mataniya, Zekariya, Yehiela,+ Abidi, Yeremoti ndi Eliya. 27 Pa ana a Zatu+ panali Elioenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza. 28 Pa ana a Bebai+ panali Yehohanani, Hananiya, Zabai ndi Atilai. 29 Pa ana a Bani panali Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubi, Seali ndi Yeremoti. 30 Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Adena, Kelali, Benaya, Maaseya, Mataniya, Bezaleli, Binui ndi Manase. 31 Pa ana a Harimu+ panali Eliezere, Isihiya, Malikiya,+ Semaya, Simeoni, 32 Benjamini, Maluki ndi Semariya. 33 Pa ana a Hasumu+ panali Matenai, Mateta, Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simeyi. 34 Pa ana a Bani panali Maadai, Amuramu, Ueli, 35 Benaya, Bedeya, Kelui, 36 Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37 Mataniya, Matenai ndi Yaasu. 38 Pa ana a Binui panali Simeyi, 39 Selemiya, Natani, Adaya, 40 Makinadebai, Sasai, Sarayi, 41 Azareli, Selemiya, Semariya, 42 Salumu, Amariya ndi Yosefe. 43 Pa ana a Nebo panali Yeyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya. 44 Onsewa anali atatenga akazi achilendo,+ ndipo akaziwo ndi ana awo anawatumiza kwawo.

[Mawu a M’munsi]

Mawu ake enieni, “anawalimbitsa manja.”

Akutchedwa “Zerubabele” pa Eza 2:2 ndi 3:8.

N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Babulo.

Akutchedwa “Yoswa” pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.

Dzina lakuti “Tirisata” ndi dzina laulemu lachiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Nthawi zambiri “dalakima” anali kuifanizira ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inali yolemera magalamu 8.4. Imeneyi si dalakima ya ku Malemba Achigiriki.

Onani Zakumapeto 12.

Akutchedwa Hodaviya pa Eza 2:40, ndipo pa Ne 7:43 akutchedwa Hodeva.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Mawu ake enieni, “timadya mchere wa kunyumba yachifumu.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Umenewu ndi udindo wa olamulira akuluakulu a zigawo za dziko.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Mawu ake enieni, “chikhomo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena