Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 2 Chronicles 1:1-36:23
  • 2 Mbiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Mbiri
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Mbiri

Mbiri Wachiwiri

1 Solomo mwana wa Davide anapitiriza kukhala wamphamvu mu ufumu wake.+ Yehova Mulungu wake anali naye,+ ndipo anapitiriza kumukulitsa kuposa wina aliyense.+

2 Tsopano Solomo anaitanitsa Aisiraeli onse, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ oweruza,+ ndi akuluakulu onse a Isiraeli+ yense, amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.+ 3 Kenako Solomo ndi mpingo wonsewo anapitira limodzi kumalo okwezeka a ku Gibeoni.+ Anapita kumeneko chifukwa ndi kumene kunali chihema chokumanako+ cha Mulungu woona, chimene Mose mtumiki+ wa Yehova anapanga m’chipululu. 4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+ 5 Ndipo guwa lansembe lamkuwa+ limene Bezaleli+ mwana wa Uri mwana wa Hura+ anapanga, anali ataliika patsogolo pa chihema chopatulika cha Yehova. Choncho Solomo ndi mpingowo anafunsira paguwalo monga mwa nthawi zonse. 6 Ndiyeno kumeneko Solomo anapereka nsembe pamaso pa Yehova paguwa lansembe lamkuwalo limene linali kuchihema chokumanako. Iye anapereka nsembe zopsereza 1,000 paguwalo.+

7 Usiku wa tsiku limenelo, Mulungu anaonekera kwa Solomo ndi kumuuza kuti: “Tandiuza, ukufuna ndikupatse chiyani?”+ 8 Solomo atamva zimenezi anauza Mulungu kuti: “Inu ndinu amene mwasonyeza kukoma mtima kosatha kwa Davide bambo anga,+ ndipo mwandiika kukhala mfumu m’malo mwake.+ 9 Tsopano inu Yehova Mulungu, kwaniritsani+ lonjezo limene munapereka kwa Davide bambo anga. Pakuti ndinu amene mwandiika kukhala mfumu+ ya anthuwa amene ndi ochuluka kwambiri ngati fumbi lapadziko lapansi.+ 10 Mundipatse nzeru ndi luntha lodziwa zinthu+ kuti ndizitha kutsogolera+ anthuwa, pakuti ndani angaweruze anthu anu ochulukawa?”+

11 Pamenepo Mulungu anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti zimenezi ndi zimene zili mumtima mwako+ ndipo sunapemphe katundu, chuma ndi ulemu kapenanso moyo wa anthu amene amadana nawe, sunapemphenso kuti ukhale ndi moyo masiku ambiri,+ koma wapempha kuti ukhale ndi nzeru ndi luntha lodziwa zinthu kuti uweruze anthu anga amene ndakupatsa kuti ukhale mfumu yawo,+ 12 upatsidwa nzeru ndi luntha lodziwa zinthu.+ Ndikupatsanso katundu, chuma, ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhale,+ ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+

13 Zitatero, Solomo anabwerera ku Yerusalemu kuchokera kumalo okwezeka a ku Gibeoni,+ kuchihema chokumanako,+ ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli.+ 14 Ndiyeno Solomo anali kusonkhanitsa magaleta* ndi mahatchi* ankhondo, moti anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi ankhondo 12,000.+ Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 15 Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva ndi golide akhale wochuluka kwambiri ngati miyala,+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu+ ya ku Sefela.+ 16 Panalinso mahatchi amene Solomo anali kugula kuchokera ku Iguputo,+ ndipo gulu la amalonda a mfumu ndilo linali kugula mahatchiwo m’magulumagulu.+ 17 Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a ku Siriya+ anali kuchitira. Mafumuwa anali kugwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.

2 Tsopano Solomo analamula kuti amange nyumba+ ya dzina la Yehova,+ ndi nyumba yachifumu ya Solomoyo.+ 2 Chotero Solomo anasankha amuna 70,000 kuti akhale onyamula katundu, ndi ena 80,000 kuti akhale osema miyala kumapiri.+ Anasankhanso amuna 3,600 kuti akhale owayang’anira.+ 3 Ndipo Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu+ mfumu ya Turo, kuti: “Monga momwe munachitira ndi Davide+ bambo anga pomawatumizira mitengo ya mkungudza kuti amangire nyumba yawo yokhalamo . . . 4 ine ndikumanga+ nyumba ya dzina+ la Yehova Mulungu wanga kuti ndiipatule+ ikhale yake. Ndikufuna kuti ndizifukiziramo mafuta onunkhira+ pamaso pake, ndi kuti nthawi zonse muzikhala mkate wosanjikiza.+ Ndiponso m’nyumbayo ndiziperekeramo nsembe zopsereza m’mawa ndi madzulo+ pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo ya zikondwerero+ za Yehova Mulungu wathu. Zimenezi zizichitika mu Isiraeli mpaka kalekale.*+ 5 Nyumba imene ndikumangayi idzakhala yogometsa,+ pakuti Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ 6 Ndipo ndani angakhale ndi mphamvu zomangira Mulunguyo nyumba?+ Pakuti kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, ndi kosakwanira kuti akhaleko.+ Ndiye ine ndine ndani+ kuti ndimumangire nyumba, kupatulapo yofukiziramo nsembe yautsi pamaso pake?+ 7 Choncho nditumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide, zasiliva, zamkuwa,+ zachitsulo, ndiponso waluso pa ntchito za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira ndi wabuluu. Munthuyo akhalenso wodziwa kujambula ndi kulemba mochita kugoba, kuti adzagwire ntchito pamodzi ndi anthu aluso amene ndili nawo kuno ku Yuda ndi ku Yerusalemu, omwe Davide bambo anga anawasankha.+ 8 Munditumizirenso matabwa a mitengo ya mkungudza,+ mitengo ina yofanana ndi mkungudza,+ ndiponso a mitengo ya m’bawa+ kuchokera ku Lebanoni,+ popeza ndikudziwa bwino kuti antchito anu ndi akatswiri odziwa kudula mitengo ya ku Lebanoni,+ (antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu,) 9 kuti andikonzere matabwa ambirimbiri, chifukwa nyumba imene ndikumanga idzakhaladi yaikulu ndi yochititsa kaso. 10 Ineyo ndipereka chakudya cha antchito anu otola nkhuni ndi odula mitengo. Ndipereka tirigu wokwanira makori* 20,000,+ balere makori 20,000, vinyo mitsuko* 20,000,+ ndi mafuta mitsuko 20,000.”

11 Hiramu mfumu ya Turo+ atamva, analemba kalata ndi kuitumiza kwa Solomo, kuti: “Popeza kuti Yehova anakonda+ anthu ake, waika inu kukhala mfumu yawo.”+ 12 Kenako Hiramu anapitiriza kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi,+ chifukwa wapereka kwa Davide mfumu mwana wanzeru, wochenjera, ndi wozindikira,+ yemwe amangire Yehova nyumba ndi kudzimangira nyumba ya ufumu wake.+ 13 Tsopano ndikutumiza munthu waluso ndi wozindikira, dzina lake Hiramu-abi.+ 14 Ameneyu ndi mwana wa mayi winawake wa fuko la Dani, koma bambo ake anali a ku Turo. Iye ndi wodziwa ntchito zagolide, zasiliva, zamkuwa,+ zachitsulo, zamiyala,+ ndi zamatabwa. Amadziwanso ntchito za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ ndi utoto wabuluu,+ komanso ntchito za nsalu+ zabwino kwambiri ndi zofiira.+ Iye amadziwanso ntchito zamtundu uliwonse zojambula ndi kulemba mochita kugoba.+ Amadziwanso ntchito zokonza zipangizo zamtundu uliwonse+ zimene angapatsidwe kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso ndi anthu aluso a mbuye wanga Davide bambo anu. 15 Ndipo tirigu, balere, mafuta, ndi vinyo, zimene inu mbuye wanga mwalonjeza, zitumizeni kwa ife akapolo anu.+ 16 Ife tidula mitengo yonse+ imene mukufunayo+ kuchokera ku Lebanoni, ndipo tiziimanga pamodzi m’maphaka oyandama n’kuitumiza kwa inu panyanja+ kukafika ku Yopa.+ Inu muzikaitengera kumeneko kupita nayo ku Yerusalemu.”

17 Kenako Solomo anawerenga amuna onse amene anali alendo m’dziko la Isiraeli.+ Anachita zimenezi pambuyo pa ntchito yowerenga alendowo imene Davide bambo ake anachita.+ Ndipo panapezeka amuna okwanira 153,600. 18 Choncho iye anasankhapo amuna 70,000 kuti akhale onyamula katundu,+ amuna 80,000 kuti akhale osema miyala+ kumapiri, ndi amuna 3,600 kuti akhale oyang’anira anthuwo pa ntchito yawo.+

3 Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu paphiri la Moriya,+ pamalo amene Yehova anaonekera kwa Davide bambo ake.+ Anamanga nyumbayo pamalo amene Davide anali atakonza. Amenewa anali malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi. 2 Iye anayamba kumanga nyumbayi m’mwezi wachiwiri pa tsiku lachiwiri, m’chaka chachinayi cha ufumu wake.+ 3 Tsopano awa ndiwo maziko amene Solomo anayala omangira nyumba ya Mulungu woona. M’litali mwa mazikowo, malinga ndi muyezo wakale, munali mikono* 60 ndipo m’lifupi mwake munali mikono 20.+ 4 Kutsata m’litali mwa nyumbayo, kumaso kwake kunali khonde+ la mikono 20 m’litali, mofanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Kuchoka pansi kufika pamwamba, khondelo linali lalitali mikono 120, ndipo mkati mwake anakutamo ndi golide woyenga bwino. 5 Nyumba yaikuluyo anaikuta+ ndi matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi zithunzi za mitengo yakanjedza+ zojambula mochita kugoba ndiponso matcheni.+ 6 Kuwonjezera apo, anakongoletsa nyumbayo+ poikuta ndi miyala yamtengo wapatali. Golide+ wakeyo anali wochokera kudziko la golide. 7 Ndipo mitanda yake ya denga,* makomo, makoma,* ndi zitseko za nyumbayo anazikuta ndi golide.+ Pamakoma ake anajambulapo akerubi mochita kugoba.+

8 Kenako anapanga chipinda cha Malo Oyera Koposa.+ M’litali mwake chinali mikono 20+ mofanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Choncho m’lifupi mwake, chipindacho chinali mikono 20, ndipo anachikuta ndi golide wabwino wokwanira matalente* 600. 9 Misomali yake inali yolemera+ masekeli* 50 agolide, ndipo zipinda zake zapadenga anazikuta ndi golide.

10 M’chipinda cha Malo Oyera Koposa anapangamo zifaniziro za akerubi+ ziwiri n’kuzikuta ndi golide.+ 11 Mapiko a akerubiwo+ kutalika kwake anali mikono 20. Phiko limodzi linali lalitali mikono isanu kufika kukhoma la chipindacho. Phiko linalo linali lalitali mikono isanu kufika paphiko la kerubi mnzake.+ 12 Phiko limodzi la kerubi wina linali lalitali mikono isanu kufika kukhoma la chipindacho, ndipo phiko linalo, lalitali mikono isanu, linali kukhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.+ 13 Mapiko a akerubiwo anali otambasuka mikono 20. Akerubiwo anali choimirira ndipo nkhope zawo zinali zitayang’ana mkati.

14 Anapanganso nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu,+ ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi nsalu yofiira komanso yabwino kwambiri. Kenako nsaluyo anaikongoletsa ndi akerubi.+

15 Ndiyeno kumaso kwa nyumbayo anamangako zipilala ziwiri+ zazitali mikono 35. Mutu+ wa chipilala chilichonse umene unali pamwamba pake unali wautali mikono isanu. 16 Atatero anapanganso matcheni+ okhala ngati ovala m’khosi ndi kuwaika kumutu kwa zipilala zija, ndipo anapanga makangaza*+ 100 n’kuwaika kumatcheniwo. 17 Zipilalazo anaziika kumaso kwa kachisi, china mbali ya kudzanja lamanja china mbali ya kumanzere. Chipilala cha mbali ya kudzanja lamanja anachitcha dzina lakuti Yakini, ndipo cha mbali ya kumanzere anachitcha dzina lakuti Boazi.+

4 Ndiyeno anapanga guwa lansembe lamkuwa.+ Guwalo linali lalikulu mikono 20 m’litali, mikono 20 m’lifupi ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba linali lalitali mikono 10.+

2 Kenako iye anapanga thanki yamkuwa.*+ Pakamwa pa thankiyo panali papakulu mikono 10 kuyeza modutsa pakati pake, ndipo panali pozungulira. Thankiyo inali yaitali mikono isanu kuchokera pansi kufika pamwamba. Pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira thankiyo.+ 3 M’munsi mwa thankiyo munali zokongoletsa zofanana ndi zipanda kuzungulira+ thankiyo, ndipo zinalipo 10 pamkono uliwonse kuzungulira thanki yonseyo.+ Zokongoletsa zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 4 Thankiyo anaikhazika pang’ombe zamphongo 12.+ Ng’ombe zitatu zinayang’ana kumpoto, zitatu zinayang’ana kumadzulo, zitatu zinayang’ana kum’mwera, ndipo zitatu zinayang’ana kum’mawa. Thankiyo inali pamwamba pa ng’ombezo ndipo mbuyo zonse za ng’ombezo zinaloza mkati.+ 5 Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi. Mlomo wake unali ngati wa mphika wakukamwa ngati duwa.+ Thankiyo inali yotha kulowa+ madzi okwana mitsuko* 3,000.+

6 Iye anapanganso mabeseni 10. Anaika mabeseni asanu mbali ya kudzanja lamanja, mabeseni asanu mbali ya kumanzere.+ M’mabeseniwo anali kutsukiramo ndi kutsukuluziramo+ zinthu zokhudzana ndi nsembe yopsereza.+ Ansembe anali kusamba madzi ochokera m’thanki ija.+

7 Kenako anapanga zoikapo nyale+ 10 zagolide zofanana,+ n’kuziika m’kachisi. Anaika zisanu mbali ya kudzanja lamanja, zisanu mbali ya kumanzere.+

8 Anapanganso matebulo 10 n’kuwaika m’kachisi. Anaika asanu mbali ya kudzanja lamanja, asanu mbali ya kumanzere,+ ndipo anapanganso mbale zolowa 100 zagolide.

9 Ndiyeno anapanga bwalo+ la ansembe+ ndi bwalo lalikulu lamkati+ ndi zitseko za bwalo lalikululo. Zitsekozo anazikuta ndi mkuwa. 10 Thanki ija anaiika mbali ya kudzanja lamanja, kum’mawa chakum’mwera.+

11 Pomalizira pake Hiramu anapanga ndowa,+ mafosholo+ ndi mbale zolowa.+

Chotero iye anamaliza ntchito imene anali kugwirira Mfumu Solomo pa nyumba ya Mulungu woona. 12 Anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yozungulira+ imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo, ndiponso maukonde awiri+ okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pamwamba pa zipilalazo. 13 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja, mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pazipilala ziwiri zija.+ 14 Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pa zotengera, 15 thanki imodzi,+ ng’ombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+ 16 ndowa, mafosholo,+ mafoloko,+ ndi ziwiya zina zonse.+ Hiramu-abivu+ anapanga zinthu zimenezi ndi mkuwa wonyezimira. Anapangira Mfumu Solomo kuti aziike m’nyumba ya Yehova. 17 Mfumuyo inaumbira zinthu zimenezi m’chikombole chochindikala chadongo, m’Chigawo* cha Yorodano, pakati pa Sukoti+ ndi Zereda.+ 18 Chotero Solomo anapanga ziwiya zimenezi zambirimbiri, moti mkuwawo sunadziwike kulemera kwake.+

19 Solomo anapanga ziwiya zonse+ zimene zinali panyumba ya Mulungu woona, guwa lansembe lagolide,+ matebulo+ oikapo mkate wachionetsero, 20 ndi zoikapo nyale+ ndi nyale zake+ zagolide woyenga bwino, zoti aziziyatsa m’chipinda chamkati+ mogwirizana ndi lamulo. 21 Anapanganso maluwa agolide, nyale zagolide, zopanira+ zagolide zozimitsira nyale, (golide wake anali woyengedwa bwino kwambiri,) 22 zozimitsira nyale, mbale zolowa, makapu, ndi zopalira moto. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.+ Anapanganso khomo lolowera m’nyumbayo,+ zitseko zamkati za Chipinda Choyera Koposa, ndi zitseko+ za nyumbayo. Zonsezi zinali zagolide.

5 Pa mapeto pake, Solomo anamaliza ntchito yonse ya panyumba ya Yehova imene anayenera kugwira.+ Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Siliva, golide, ndi ziwiya zonse anaziika mosungira chuma cha panyumba ya Mulungu woona.+ 2 Pa nthawi imeneyo m’pamene Solomo anauza akulu a Isiraeli,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a nyumba za makolo+ a ana a Isiraeli kuti asonkhane ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa+ la pangano la Yehova ku+ Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+ 3 Choncho anthu onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa mfumu pachikondwerero cha m’mwezi wa 7.+

4 Akulu onse a Isiraeli anabwera,+ ndipo Alevi anayamba kunyamula Likasa.+ 5 Ansembe achilevi+ ananyamula Likasa,+ chihema chokumanako,+ ndi ziwiya zonse zopatulika+ zimene zinali m’chihemacho. 6 Mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Aisiraeli, onse amene anabwera atawaitana, anafika pamaso pa Likasa n’kuyamba kupereka nsembe+ zambiri za nkhosa ndi ng’ombe, zomwe sanathe kuziwerenga chifukwa chochuluka. 7 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova kumalo ake, kuchipinda chamkati+ cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa,+ ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+ 8 Mapiko a akerubiwo anali otambasukira pamwamba pa malo okhala Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba+ pa Likasa ndi pamwamba pa mitengo yake yonyamulira.+ 9 Koma mitengo yonyamulirayo inali yaitali, moti nsonga zake zinali kuonekera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinali kuoneka kunja. Mitengo yonyamulirayo ikadali pomwepo mpaka lero.+ 10 Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo ku Horebe.+ Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+

11 Tsopano ansembe anatuluka m’malo oyera (chifukwa ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa+ ndipo panalibe chifukwa choti atumikire motsatira magulu awo).+ 12 Ndipo Alevi+ oimba a m’gulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni,+ ana awo ndi abale awo, onsewa atavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe+ ndi azeze,+ anaimirira kum’mawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwanira 120 oimba malipenga.+ 13 Tsopano anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana+ n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba+ ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbira zina potamanda+ Yehova ndi mawu akuti, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha+ kudzakhala mpaka kalekale.” Kenako mtambo unadzaza nyumbayo,+ nyumba ya Yehova.+ 14 Chifukwa cha mtambowo,+ ansembewo analephera kupitiriza kutumikira, popeza ulemerero+ wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.

6 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anati:+ “Yehova anati adzakhala mumdima wandiweyani.+ 2 Koma ine ndakumangirani nyumba yomwe ndi malo anu okhalamo okwezeka,+ malo okhazikika oti mukhalemo mpaka kalekale.”+

3 Kenako mfumu inatembenuka n’kuyang’ana anthuwo. Ndiyeno inayamba kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli. Pamenepo n’kuti mpingo wonse wa Isiraeli utaimirira.+ 4 Mfumuyo inapitiriza kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analankhula ndi pakamwa pake kwa Davide bambo anga,+ ndipo ndi manja ake wakwaniritsa+ zimene ananena, kuti, 5 ‘Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa anthu anga m’dziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda m’mafuko onse a Isiraeli woti iwo amangeko nyumba ya dzina langa+ kuti likhale kumeneko, ndipo sindinasankhe munthu woti akhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ 6 Koma ndidzasankha Yerusalemu+ kuti dzina langa likhale kumeneko, ndiponso ndidzasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+ 7 Ndipo bambo anga Davide, anafuna mumtima mwawo kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 8 Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Popeza unafuna mumtima mwako kumanga nyumba ya dzina langa, unachita bwino chifukwa unafuna mumtima mwako kuchita zimenezi.+ 9 Koma iweyo sumanga nyumbayi,+ m’malomwake mwana wako wamwamuna wotuluka m’chiuno mwako ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 10 Yehova anakwaniritsa mawu+ amene ananena, kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga+ n’kukhala pampando wachifumu+ wa Isiraeli, monga momwe Yehova ananenera,+ ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 11 Komanso kuti m’nyumbamo ndiikemo Likasa,+ lomwe muli pangano la Yehova limene anapangana ndi ana a Isiraeli.”+

12 Tsopano Solomo anaimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli.+ Kenako anatambasula manja ake.+ 13 (Pakuti Solomo anapanga nsanja+ yamkuwa n’kuiika pakati pa bwalo lamkati.+ Nsanjayo inali yaikulu mikono isanu m’litali, mikono isanu m’lifupi, ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba inali yaitali mikono itatu. Iye anaimirira pansanjayo.) Atatero anagwada+ patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli. Kenako anatambasula manja ake n’kuwakweza kumwamba.+ 14 Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse, inu mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.+ 15 Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga.+ Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 16 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako+ asamale mayendedwe awo mwa kuyenda motsatira malamulo anga+ monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’+ 17 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ lonjezo lanu+ limene munalonjeza mtumiki wanu Davide likwaniritsidwe.+

18 “Koma kodi Mulungu angakhaledi ndi anthu padziko lapansi?+ Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?+ 19 Mutembenukire ku pemphero la mtumiki wanu+ ndi pempho lake lopempha chifundo,+ inu Yehova Mulungu wanga. Mverani kulira kwanga kochonderera+ ndi pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu.+ 20 Maso anu akhale akuyang’ana+ nyumba ino usana ndi usiku. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti mudzaikako dzina lanu,+ mwa kumvetsera pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana malo ano.+ 21 Mumve mapemphero ochonderera a mtumiki+ wanu ndi a anthu anu Aisiraeli, pamene akupemphera atayang’ana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+

22 “Munthu akachimwira mnzake+ n’kuchita lumbiro lokhala ndi temberero+ potsimikiza kuti sanachimwe, iye n’kubwera pamaso pa guwa lansembe m’nyumba ino ali pansi pa tembererolo,+ 23 inu mumve muli kumwamba+ ndipo muchitepo kanthu+ mwa kusonyeza amene ali wolakwa pom’bwezera temberero lake,+ ndi kusonyeza amene ali wolungama+ pom’patsa mphoto malinga ndi chilungamo chake.+

24 “Anthu anu Aisiraeli akagonja kwa mdani wawo+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno akabwerera+ kwa inu n’kutamanda dzina lanu+ ndi kupemphera+ ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo pamaso panu m’nyumba ino,+ 25 inuyo mumve muli kumwamba+ ndipo mukhululuke+ tchimo la anthu anu Aisiraeli, ndi kuwabwezeretsa+ kudziko limene munapatsa iwo ndi makolo awo.+

26 “Kumwamba kukatsekeka, mvula n’kumakanika kugwa+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno iwo n’kupemphera atayang’ana malo ano,+ ndi kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya tchimo lawo chifukwa choti mwakhala mukuwasautsa,+ 27 inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisiraeli, popeza mumawaphunzitsa+ njira yabwino+ yoti ayendemo. Mubweretse mvula+ padziko lanu, limene mwapatsa anthu anu monga cholowa.+

28 “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu,+ matenda a mbewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani+ awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo,+ ndiponso kukagwa mliri wamtundu wina uliwonse, nthenda yamtundu wina uliwonse,+ 29 ndiyeno anthuwo akapereka pemphero lililonse,+ pempho lililonse lopempha chifundo+ limene munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli+ angapemphe, chifukwa aliyense wa iwo akudziwa mliri wake+ ndi ululu wake, ndipo aliyense akatambasula manja ake kuwalozetsa kunyumba ino,+ 30 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu).+ 31 Muchite zimenezi n’cholinga choti iwo akuopeni,+ mwa kuyenda m’njira zanu masiku onse amene angakhale ndi moyo padziko limene munapatsa makolo athu.+

32 “Komanso mlendo amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli,+ amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu,+ ndi dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka,+ ndipo iwo abwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+ 33 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni+ mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+

34 “Anthu anu akapita ku nkhondo+ kukamenyana ndi adani awo kumene inuyo mwawatumiza,+ ndipo akapemphera+ kwa inu atayang’ana kumzinda umene mwasankha ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 35 inuyo mumve muli kumwamba pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+

36 “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa mdani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 37 ndiyeno iwo akazindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo n’kulapa, ndipo akapempha chifundo kwa inu m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 38 n’kubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ m’dziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayang’ana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, kumzinda umene mwasankha+ ndiponso kunyumba ya dzina lanu imene ndamangayi,+ 39 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.+ Mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+ Mukhululukire+ anthu anu amene akuchimwirani.

40 “Tsopano Mulungu wanga, chonde, maso anu aone,+ ndipo makutu anu+ akhale tcheru kumvetsera pemphero lokhudza malo ano. 41 Tsopano inu Yehova Mulungu nyamukani+ mulowe mu mpumulo wanu,+ inuyo ndi Likasa limene mumasonyezera mphamvu zanu.+ Ansembe anu, inu Yehova Mulungu, avale chipulumutso ndipo okhulupirika anu asangalale chifukwa cha zabwino.+ 42 Inu Yehova Mulungu, musakane wodzozedwa wanu.+ Musaiwale kukoma mtima kosatha kumene munasonyeza Davide mtumiki wanu.”+

7 Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba.+ Motowo unanyeketsa nsembe yopsereza+ pamodzi ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova+ unadzaza nyumbayo. 2 Chotero ansembe sanathe kulowa m’nyumba ya Yehova+ chifukwa ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova. 3 Ana onse a Isiraeli anali kuonerera pamene moto unali kutsika, ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unaonekera pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, nthawi yomweyo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ ndi kuyamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+

4 Kenako mfumuyo ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.+ 5 Mfumu Solomo inapereka nsembe ya ng’ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000.+ Choncho mfumuyo ndi anthu onse anatsegulira+ nyumba ya Mulungu woona. 6 Ansembe+ anali ataimirira m’malo awo a ntchito pamodzi ndi Alevi,+ onse atanyamula zipangizo zoimbira+ Yehova nyimbo zimene Davide+ mfumu anapanga kuti aziyamikira Yehova. Aleviwo anali kunena kuti “pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.” Iwo ankanena zimenezi paliponse pamene Davide akanatamanda Mulungu kudzera mwa iwo. Ansembe anali kuimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.

7 Solomo anapatula+ malo a pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova, chifukwa pamenepo anaperekerapo nsembe zopsereza,+ ndi mafuta a nsembe zachiyanjano. Anatero popeza guwa lansembe lamkuwa+ limene iye anamanga linachepa, ndipo sipakanakwana nsembe yopsereza, nsembe yambewu,+ ndi mafuta oundana.+ 8 Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero+ masiku 7 pamodzi ndi Aisiraeli onse.+ Unali mpingo waukulu+ wa anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira polowera ku Hamati+ n’kutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ 9 Koma pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera+ chifukwa kwa masiku 7 anali kutsegulira guwa lansembe ndipo kwa masiku 7 ena anali kuchita chikondwerero. 10 Pa tsiku la 23 la mwezi wa 7, Solomo anauza anthuwo kuti azipita kwawo. Iwo anapita akusangalala+ komanso akumva bwino mumtima, chifukwa cha zabwino+ zimene Yehova anachitira Davide, Solomo, ndiponso zimene anachitira anthu ake Aisiraeli.+

11 Choncho Solomo anamaliza kumanga nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu.+ Zilizonse zimene iye anaganiza kuchita mumtima mwake zokhudza nyumba ya Yehova ndi nyumba yake zinayenda bwino. 12 Kenako Yehova anaonekera+ kwa Solomo usiku n’kumuuza kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndipo ndasankha+ malo ano kukhala nyumba yanga yoperekeramo nsembe.+ 13 Ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe,+ ndikalamula dzombe kuti lidye zomera za m’dzikoli,+ ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga,+ 14 ndipo anthu anga+ otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa+ n’kupemphera,+ n’kufunafuna nkhope yanga,+ n’kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba+ n’kuwakhululukira tchimo lawo+ ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+ 15 Tsopano maso anga+ akhala otseguka ndipo makutu anga+ azimvetsera mapemphero onenedwa pamalo ano. 16 Ndasankha+ ndi kuyeretsa nyumba ino kuti dzina langa+ likhale pamenepa mpaka kalekale,+ ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepa nthawi zonse.+

17 “Iweyo ukayenda pamaso panga monga momwe Davide+ bambo ako anayendera, mwa kuchita zonse zimene ndakulamula+ ndi kusunga malangizo anga+ ndi zigamulo zanga,+ 18 inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu,+ monga momwe ndinapanganirana ndi Davide bambo ako+ kuti, ‘Munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ 19 Koma inuyo mukadzabwerera+ n’kusiya kutsatira malamulo anga+ amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina+ ndi kuigwadira,+ 20 ineyo ndidzakuchotsani padziko langa limene ndakupatsani+ ndipo nyumba iyi yomwe ndaiyeretsa+ chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Ndidzachititsa anthu kuipekera mwambi+ ndi kuitonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.+ 21 Ndipo nyumba iyi ikadzakhala bwinja,+ aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa,+ ndipo ndithu adzati, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+ 22 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira.+ N’chifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+

8 Kumapeto kwa zaka 20+ zimene Solomo anamanga nyumba ya Yehova+ ndi nyumba yake,+ 2 iye anamanganso mizinda imene Hiramu+ anam’patsa n’kuipereka kwa Aisiraeli kuti azikhalamo. 3 Kuwonjezera pamenepo, Solomo anapita ku Hamati-zoba n’kugonjetsa mzindawo. 4 Kenako anamanganso mzinda wa Tadimori m’chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo zinthu+ imene anamanga ku Hamati.+ 5 Ndiyeno anamanga mzinda wa Beti-horoni Wakumtunda+ ndi Beti-horoni Wakumunsi.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ zitseko ndi mipiringidzo.+ 6 Anamanganso Baalati+ ndi mizinda yonse yosungirako zinthu imene inakhala ya Solomo, mizinda yonse yosungirako magaleta,+ mizinda yonse ya amuna okwera pamahatchi,+ ndi chilichonse chimene iye anakonda+ kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni,+ ndi m’dziko lonse limene ankalamulira.

7 Anthu onse otsala a Ahiti,+ Aamori,+ Aperezi,+ Ahivi,+ ndi Ayebusi,+ amene sanali Aisiraeli,+ 8 ana onse ochokera kwa iwowa amene anatsala m’dzikomo, amene ana a Isiraeli sanawawononge,+ Solomo anali kuwagwiritsa+ ntchito yaukapolo, kufikira lero.+ 9 Koma panalibe ana a Isiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo ogwira ntchito yake,+ chifukwa iwo anali ankhondo ake,+ atsogoleri a asilikali ake othandiza pamagaleta, atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta+ ndiponso a amuna ake okwera pamahatchi.+ 10 Panali akuluakulu oyang’anira nduna+ okwana 250 a Mfumu Solomo. Iwowa anali akapitawo oyang’anira anthu ogwira ntchito.+

11 Solomo anatulutsa mwana wamkazi wa Farao+ mu Mzinda wa Davide+ n’kukamuika m’nyumba imene anam’mangira,+ pakuti iye anati: “Ngakhale ali mkazi wanga, asamakhale m’nyumba ya Davide mfumu ya Isiraeli, chifukwa malo alionse amene likasa la Yehova likukhala ndi oyera.”+

12 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anapereka nsembe yopsereza+ kwa Yehova paguwa lansembe+ la Yehova limene iye anamanga patsogolo pa khonde.+ 13 Anapereka nsembezo mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku+ loperekera nsembe, malinga ndi chilamulo cha Mose. Nsembezo zinali za pa masabata,+ za pa masiku okhala mwezi,+ ndi za pa zikondwerero zoikidwiratu+ zochitika katatu pa chaka.+ Zikondwererozo zinali chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata,+ ndi chikondwerero cha misasa.+ 14 Kuwonjezera pamenepo, Solomo anaika magulu+ a ansembe pa utumiki wawo mogwirizana ndi lamulo la Davide bambo ake.+ Anaikanso Alevi+ pamalo awo a ntchito kuti azitamanda+ ndi kutumikira+ pamaso pa ansembe mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku.+ Komanso anaika alonda a pazipata m’magulu awo kuti akhale m’zipata zosiyanasiyana+ chifukwa ndilo linali lamulo la Davide munthu wa Mulungu woona. 15 Iwo sanapatuke pa lamulo limene mfumu inapereka kwa ansembe ndi kwa Alevi lokhudza nkhani ina iliyonse ndi zinthu zina zofunikira.+ 16 Choncho ntchito yonse ya Solomo, kuyambira pa tsiku limene anayala+ maziko a nyumba ya Yehova kufikira pamene inatha,+ inayenda bwino. Motero nyumba ya Yehova inatha kumangidwa.+

17 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anapita ku Ezioni-geberi+ ndi ku Eloti,+ kugombe la nyanja m’dziko la Edomu.+ 18 Hiramu,+ kudzera mwa antchito ake, ankatumizira Solomo zombo ndi antchito odziwa za panyanja.+ Iwo ankapita ku Ofiri+ pamodzi ndi antchito a Solomo kukatenga golide+ wokwana matalente* 450,+ ndipo anali kubwera naye kwa Mfumu Solomo.+

9 Mfumukazi ya ku Sheba+ inamva za Solomo. Choncho inabwera ku Yerusalemu kuti idzamuyese Solomo pomufunsa mafunso ovuta.+ Mfumukaziyo inabwera ndi anthu oiperekeza ambiri, ndiponso ngamila+ zitanyamula mafuta a basamu,+ golide+ wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Inafika kwa Solomo n’kuyamba kumuuza zonse zimene zinali kumtima kwake.+ 2 Solomo anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse.+ Panalibe chimene Solomo analephera kuyankha.+

3 Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+ 4 chakudya cha patebulo pake,+ mmene atumiki ake anali kukhalira pa nthawi ya chakudya, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuchitira, zovala zawo,+ anthu ake operekera zakumwa+ ndi zovala zawo, ndi nsembe zake zopsereza+ zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse,+ inazizira nkhongono ndipo inasowa chonena. 5 Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani za zochita zanu ndi nzeru zanu zimene ndinamva kudziko langa, n’zoonadi.+ 6 Sindinakhulupirire+ mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga,+ ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe ya nzeru zanu zochuluka.+ Mwaposa zinthu zimene ndinamva.+ 7 Odala+ anthu anu, odala atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.+ 8 Adalitsike Yehova Mulungu wanu,+ amene wasangalala+ nanu mwa kukuikani pampando wake wachifumu+ monga mfumu yolamulira m’malo mwa Yehova Mulungu wanu.+ Popeza Mulungu wanu anakonda+ Isiraeli kuti akhalepo mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu yawo,+ kuti muzipereka zigamulo+ ndi kuchita chilungamo.”+

9 Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.+

10 Kuwonjezera pamenepo, atumiki a Hiramu+ ndi atumiki a Solomo amene anabwera ndi golide+ kuchokera ku Ofiri, anabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ndi miyala yamtengo wapatali.+ 11 Mfumuyo inapanga masitepe a nyumba ya Yehova ndi a nyumba ya mfumu+ pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo.+ Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba.+ Zinthu zamtundu umenewu zinali zisanaonekepo m’dziko la Yuda.

12 Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi+ ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha. Solomo anapatsa mfumukaziyo zinthu zoposa zimene inabweretsa kwa iye. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+

13 Golide amene ankabwera kwa Solomo chaka chimodzi, anali wolemera matalente 666,*+ 14 osawerengera golide wa amalonda oyendayenda,+ amalonda ena amene anali kubweretsa katundu, mafumu onse a Aluya,+ ndi abwanamkubwa a m’dzikolo amene anali kubweretsa golide ndi siliva kwa Solomo.

15 Mfumu Solomo inapanga zishango 200 zikuluzikulu zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chachikulu chilichonse anachikuta ndi golide wosakaniza ndi zitsulo zina wolemera masekeli 600.)+ 16 Inapanganso zishango 300 zing’onozing’ono zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chaching’ono chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.)+ Kenako mfumuyo inaika zishangozi m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+

17 Itatero, mfumuyo inapanga mpando wachifumu waukulu wa minyanga ya njovu, n’kuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 18 Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Mpando wachifumuwo unali ndi chopondapo mapazi chagolide (ziwirizi zinali zolumikizana). Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira.+ 19 Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango+ itaimirira, mbali iyi ndi iyi. Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.+ 20 Ziwiya zonse zomweramo+ Mfumu Solomo zinali zagolide,+ ndipo ziwiya zonse za m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali zagolide woyenga bwino. Panalibe chiwiya chasiliva. Siliva sankaoneka ngati kanthu+ m’masiku a Solomo, 21 pakuti zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide, siliva,+ minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.+

22 Chotero Mfumu Solomo inali yolemera kwambiri+ ndiponso yanzeru kwambiri+ kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 23 Mafumu onse a padziko lapansi ankafuna kuonana+ ndi Solomo, kuti amve nzeru zake+ zimene Mulungu woona anaika mumtima mwake.+ 24 Aliyense anali kubweretsa mphatso+ chaka chilichonse monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide,+ zovala,+ zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi, ndi nyulu.*+ 25 Solomo anakhala ndi makola 4,000 a mahatchi.+ Analinso ndi magaleta+ ndi mahatchi ankhondo okwana 12,000. Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 26 Solomo anakhala wolamulira wa mafumu onse kuyambira ku Mtsinje* mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo.+ 27 Kuwonjezera apo, mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva akhale wochuluka kwambiri ngati miyala, ndiponso kuti matabwa a mkungudza+ akhale ochuluka kwambiri+ ngati mitengo ya mkuyu ya ku Sefela.+ 28 Anthu anali kubweretsa mahatchi+ kwa Solomo kuchokera ku Iguputo+ ndi mayiko ena onse.

29 Nkhani zina zokhudza Solomo,+ zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’mawu a mneneri Natani.+ Zalembedwanso mu ulosi wa Ahiya+ Msilo,+ ndiponso m’buku la masomphenya a Ido+ wamasomphenya, lonena za Yerobowamu+ mwana wa Nebati.+ 30 Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu zaka 40. 31 Pomalizira pake Solomo anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide bambo ake.+ Kenako mwana wake Rehobowamu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+

10 Tsopano Rehobowamu+ anapita ku Sekemu,+ chifukwa kumeneko n’kumene Aisiraeli onse anasonkhana kuti akamulonge ufumu. 2 Yerobowamu+ mwana wa Nebati atamva zimenezi ali ku Iguputo,+ (pajatu anathawa mfumu Solomo,) nthawi yomweyo anabwerera kuchokera ku Iguputoko.+ 3 Choncho anthu anatumiza uthenga womuitana, ndipo Yerobowamu ndi Aisiraeli onse anabwera n’kuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:+ 4 “Bambo anu anaumitsa goli lathu.+ Tsopano inuyo mufewetse ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera+ limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”+

5 Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye kwa masiku atatu, ndipo mukabwerenso kwa ine.” Anthuwo anapitadi. 6 Ndiyeno Mfumu Rehobowamu inafunsira nzeru+ kwa akulu amene anali kutumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Inawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”+ 7 Iwo anaiuza kuti: “Mukakhala munthu wabwino kwa anthuwa ndi kuchita zowasangalatsa, ndiponso mukawayankha ndi mawu abwino,+ iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”+

8 Koma iye sanamvere malangizo+ ochokera kwa akulu aja, m’malomwake anayamba kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi,+ omwe anali kum’tumikira.+ 9 Iye anawafunsa kuti: “Kodi mungapereke malangizo+ otani kuti tiwayankhe anthuwa amene andipempha kuti, ‘Fewetsani goli limene bambo anu anatisenzetsa’?”+ 10 Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Izi n’zimene mukanene kwa anthu awa amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsireko.’ Muwauze kuti,+ ‘Chala changa chaching’ono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga.+ 11 Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo.+ Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”+

12 Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, monga momwe mfumuyo inanenera kuti: “Mukabwerenso kwa ine pa tsiku lachitatu.”+ 13 Mfumuyo inayamba kuyankha anthuwo mwaukali.+ Chotero Mfumu Rehobowamu inasiya malangizo+ a akulu aja.+ 14 Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja anaipatsa.+ Inati: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemera kwambiri, ndipo ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+ 15 Mfumuyo sinamvere anthuwo chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Mulungu woona,+ kuti Yehova akwaniritse mawu ake+ amene analankhula kwa Yerobowamu mwana wa Nebati,+ kudzera mwa Ahiya+ Msilo.+

16 Popeza kuti mfumuyo sinawamvere Aisiraeli onsewo, iwo anayankha mfumuyo kuti: “Tili ndi gawo lanji mwa Davide?+ Ife tilibe cholowa mwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu yake!+ Tsopano iwe Davide,+ uzisamalira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, onse anayamba kubwerera kumahema awo.

17 Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira ana a Isiraeli amene anali kukhala m’mizinda ya ku Yuda.+

18 Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Hadoramu+ amene anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yokakamiza, koma ana a Isiraeli anam’ponya miyala+ n’kumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inakwanitsa kukwera galeta lake n’kuthawira ku Yerusalemu.+ 19 Ndipo Aisiraeli anapitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.

11 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000+ a nyumba yonse ya Yuda ndi ya Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu. 2 Kenako mawu a Yehova anafikira Semaya+ munthu wa Mulungu woona, kuti: 3 “Kauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda,+ ndi Aisiraeli onse ku Yuda ndi ku Benjamini, kuti, 4 ‘Yehova wati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”’”+ Choncho anamvera mawu a Yehova n’kubwerera, osakamenyana ndi Yerobowamu.+

5 Rehobowamu anapitiriza kukhala ku Yerusalemu, ndipo anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri m’dziko la Yuda. 6 Anamanganso mizinda ya Betelehemu,+ Etami,+ Tekowa,+ 7 Beti-zuri,+ Soko,+ Adulamu,+ 8 Gati,+ Maresha,+ Zifi,+ 9 Adoraimu, Lakisi,+ Azeka,+ 10 Zora,+ Aijaloni+ ndi Heburoni.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri imene inali ku Yuda ndi ku Benjamini. 11 Kuwonjezera apo, analimbitsanso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ n’kuikamo atsogoleri.+ Atatero m’mizindamo anaikamo chakudya, mafuta ndi vinyo. 12 M’mizinda yonse yosiyanasiyana anaikamo zishango zazikulu+ ndi mikondo ing’onoing’ono.+ Mizindayo anailimbitsa kwambiri, ndipo iye anapitiriza kulamulira Yuda ndi Benjamini.

13 Ansembe ndi Alevi m’madera awo onse mu Isiraeli yense, anakhala kumbali ya Rehobowamu. 14 Aleviwo anasiya malo awo odyetserako ziweto+ ndi madera awo+ n’kupita ku Yuda ndi ku Yerusalemu,+ chifukwa Yerobowamu+ ndi ana ake anachotsa+ Aleviwo pa udindo wokhala ansembe a Yehova. 15 Iye anadziikira ansembe m’malo okwezeka+ kuti azitumikira ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga.+ 16 Koma anthu a m’mafuko onse a Isiraeli amene anali ndi mtima wofunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anatsatira ansembe ku Yerusalemu+ kukapereka nsembe+ kwa Yehova Mulungu wa makolo awo. 17 Iwo analimbitsa ufumu wa Yuda+ ndi kulimbikitsa Rehobowamu mwana wa Solomo kwa zaka zitatu, popeza anthuwo anayenda m’njira ya Davide ndi ya Solomo kwa zaka zitatu.+

18 Rehobowamu anakwatira Mahalati mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide. Amayi ake a Mahalati anali Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu+ mwana wa Jese. 19 M’kupita kwa nthawi, Mahalatiyo anaberekera Rehobowamu ana. Anawo anali Yeusi, Semariya ndi Zahamu. 20 Pambuyo pake Rehobowamu anakwatira Maaka+ mdzukulu wa Abisalomu.+ Kenako mkaziyo anam’berekera ana awa: Abiya,+ Atai, Ziza ndi Selomiti. 21 Rehobowamu anali kukonda kwambiri Maaka mdzukulu wa Abisalomu kuposa akazi ake ena onse+ ndi adzakazi* ake, pakuti iye anakwatira akazi 18, ndiponso anali ndi adzakazi 60. Iye anabereka ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60. 22 Chotero Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri wa abale ake. Anatero chifukwa iye ankafuna kuti adzam’patse ufumu. 23 Komabe anachita mozindikira+ chifukwa anagawa ana akewo n’kuwaika m’madera onse a ku Yuda ndi ku Benjamini.+ Anawaika m’mizinda yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ ndipo anawapatsa chakudya chambiri+ ndi kuwapezera akazi ambirimbiri.+

12 Ufumu wa Rehobowamu utangokhazikika+ ndiponso iye atangokhala wamphamvu, iye ndi Aisiraeli onse+ anasiya chilamulo cha Yehova.+ 2 M’chaka chachisanu cha Mfumu Rehobowamu,+ Sisaki+ mfumu ya Iguputo anabwera kudzaukira Yerusalemu (chifukwa iwo anachita zosakhulupirika kwa Yehova).+ 3 Anabwera ndi magaleta 1,200+ ndi amuna okwera pamahatchi 60,000. Anabweranso ndi anthu osawerengeka+ kuchokera ku Iguputo. Anthuwo anali Alibiya,+ Asuki ndi Aitiyopiya.+ 4 Sisakiyo analanda mizinda ya Yuda+ yomwe inali ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo pamapeto pake anafika ku Yerusalemu.+

5 Tsopano mneneri Semaya+ anapita kwa Rehobowamu ndi kwa akalonga a Yuda amene anasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisaki. Iye anawauza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Inuyo mwandisiya,+ choncho inenso ndakusiyani+ ndipo ndakuperekani m’manja mwa Sisaki.’” 6 Akalonga a Isiraeliwo ndi mfumuyo atamva zimenezi, anadzichepetsa+ n’kunena kuti: “Yehova ndi wolungama.”+ 7 Yehova ataona+ kuti anthuwo adzichepetsa, mawu a Yehova anafika kwa Semaya,+ kuti: “Anthuwa adzichepetsa,+ choncho sindiwawononga. Posachedwapa ndiwapulumutsa, ndipo sinditsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu kudzera m’manja mwa Sisaki.+ 8 Koma iwo akhala atumiki ake+ kuti adziwe kusiyana kokhala atumiki anga+ ndi kokhala atumiki a maufumu a m’dzikoli.”+

9 Chotero Sisaki+ mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu ndi kutenga chuma cha m’nyumba ya Yehova+ ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomo anapanga.+ 10 Choncho Mfumu Rehobowamu inapanga zishango zamkuwa m’malo mwake, ndipo inazipereka kwa akulu a asilikali othamanga,+ omwe anali alonda+ a pakhomo la nyumba ya mfumu, kuti aziziyang’anira.+ 11 Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikali othamangawo ankanyamula zishangozo, ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.+ 12 Chifukwa chakuti Rehobowamu anadzichepetsa, Yehova anabweza mkwiyo wake+ ndipo sanaganizenso zoti awawononge anthu onsewo.+ Komanso mwa anthu a ku Yuda munapezeka ntchito zabwino.+

13 Mfumu Rehobowamu inapitiriza kulimbitsa ufumu wake ndi kulamulira ku Yerusalemu. Rehobowamu+ anali ndi zaka 41 pamene anayamba kulamulira, ndipo kwa zaka 17 analamulira ku Yerusalemu, mzinda+ umene Yehova anasankha pakati pa mafuko onse a Isiraeli kuti aike dzina lake kumeneko.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama+ Muamoni.+ 14 Koma iye anachita zoipa+ chifukwa sanatsimikize kufunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.+

15 Nkhani zina zokhudza Rehobowamu, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’mawu a mneneri Semaya+ ndiponso m’mawu a Ido+ wamasomphenya, motsatira mndandanda wa mayina a makolo. Nthawi zonse panali kuchitika nkhondo pakati pa Rehobowamu+ ndi Yerobowamu.+ 16 Pomalizira pake, Rehobowamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Abiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

13 M’chaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu, Abiya anayamba kulamulira Yuda.+ 2 Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Mikaya+ mwana wa Uriyeli wa ku Gibeya.+ Kenako pakati pa Abiya ndi Yerobowamu panachitika nkhondo.+

3 Choncho Abiya anapita kukamenya nkhondoyo ndi gulu la amuna amphamvu ankhondo+ osankhidwa mwapadera okwanira 400,000. Yerobowamu nayenso anapita kukamenyana ndi Abiya ndipo anapita ndi asilikali 800,000. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima osankhidwa mwapadera, ndipo anakafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ 4 Tsopano Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu limene lili m’dera lamapiri la Efuraimu,+ n’kunena kuti: “Tamvera, iwe Yerobowamu ndi Aisiraeli onsewo. 5 Kodi simukudziwa kuti Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka ufumu kwa Davide+ kuti azilamulira Isiraeli mpaka kalekale?+ Simukudziwa kodi kuti anaupereka kwa iye ndi ana ake+ pochita naye pangano losatha?*+ 6 Koma Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anali mtumiki+ wa Solomo mwana wa Davide, anapanduka+ n’kuukira mbuye wake.+ 7 Ndipo anthu osowa chochita+ ndi opanda pake+ anasonkhana kumbali yake. Pamapeto pake iwo anakhala amphamvu kuposa Rehobowamu+ mwana wa Solomo pamene Rehobowamuyo anali wamng’ono komanso wamantha,+ ndipo sanathe kulimbana nawo.

8 “Tsopano anthu inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Yehova umene uli m’manja mwa ana a Davide,+ popeza ndinu khamu lalikulu+ ndipo muli ndi ana a ng’ombe agolide amene Yerobowamu anakupangirani kuti akhale milungu yanu.+ 9 Kodi simunathamangitse ansembe a Yehova,+ omwe ndi ana a Aroni, komanso Alevi? Ndipo kodi simukudziikira ansembe ngati mmene amachitira anthu a mayiko ena?+ Aliyense amene wabwera n’kudziika pa udindo waunsembe mwa kupereka ng’ombe yaing’ono yamphongo ndi nkhosa zamphongo 7, amakhala wansembe wa mafano omwe si milungu.+ 10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu+ ndipo sitinamusiye. Ansembe, omwe ndi ana a Aroni, akutumikira Yehova, ndiponso Alevi akugwira ntchito yawo.+ 11 Iwo akufukiza nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa uliwonse ndi madzulo alionse.+ Akufukizanso mafuta onunkhira+ ndipo mikate yosanjikiza ili patebulo la golide woyenga bwino.+ Tilinso ndi choikapo nyale chagolide+ ndi nyale zake zimene amayatsa madzulo alionse.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu+ kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.+ 12 Taonani, ife patsogolo pathu pali Mulungu woona+ ndi ansembe ake,+ ndi malipenga+ otiitanira ku nkhondo yomenyana nanu. Inu ana a Isiraeli, musamenyane ndi Yehova Mulungu wa makolo anu,+ chifukwa simupambana.”+

13 Pamenepo Yerobowamu anatumiza asilikali kuti akawabisalire kumbuyo, choncho Yerobowamuyo ndi asilikali ake anakhala kutsogolo kwa Ayuda ndipo obisalawo anali kumbuyo kwa Ayudawo.+ 14 Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo.+ Choncho anayamba kufuulira Yehova+ pamene ansembe anali kuliza malipenga mokweza. 15 Kenako amuna a Yuda anayamba kufuula mfuu ya nkhondo.+ Atafuula mfuu ya nkhondoyo, Mulungu woona anagonjetsa+ Yerobowamu ndi Aisiraeli onse pamaso pa Abiya+ ndi Ayuda. 16 Kenako ana a Isiraeli anayamba kuthawa pamaso pa Ayuda, koma Mulungu anawapereka m’manja mwa Ayudawo.+ 17 Abiya ndi anthu ake anapha Aisiraeli ambirimbiri. Aisiraeliwo anapitirira kuphedwa mpaka ophedwawo anakwana amuna 500,000 osankhidwa mwapadera. 18 Choncho ana a Isiraeli anachititsidwa manyazi pa nthawi imeneyo, koma ana a Yuda anapambana chifukwa anadalira+ Yehova Mulungu wa makolo awo. 19 Abiya anapitiriza kuthamangitsa Yerobowamu ndipo anamulanda mizinda yake. Analanda Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, Yesana ndi midzi yake yozungulira, ndiponso Efuraini ndi midzi yake yozungulira.+ 20 Yerobowamu sanakhalenso ndi mphamvu+ m’masiku a Abiya, ndipo Yehova anamukantha+ moti anafa.

21 Abiya anapitiriza kulimbitsa ufumu wake.+ M’kupita kwa nthawi, anakwatira akazi 14+ ndipo anabereka ana aamuna 22+ ndi aakazi 16. 22 Nkhani zina zokhudza Abiya, njira zake ndi mawu ake, zinalembedwa m’buku la ndemanga la mneneri Ido.+

14 Pomalizira pake, Abiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Asa+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. M’masiku ake, m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse+ kwa zaka 10.

2 Asa anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake. 3 Choncho iye anachotsa maguwa ansembe achilendo,+ anagwetsa malo okwezeka,+ anaphwanya zipilala zopatulika+ ndi kudula mizati yopatulika.+ 4 Kuwonjezera apo, anauza Ayuda kuti afunefune+ Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo.+ 5 Iye anachotsa malo okwezeka ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira+ m’mizinda yonse ya Yuda, ndipo ufumuwo unapitiriza kukhala wopanda chosokoneza chilichonse+ mu ulamuliro wake. 6 Kenako anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri m’dziko la Yuda,+ chifukwa m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse, komanso palibe anachita naye nkhondo pa zaka zimenezi, chifukwa Yehova anam’patsa mpumulo.+ 7 Choncho iye anauza Ayuda kuti: “Tiyeni timange mizindayi ndi mipanda+ yoizungulira. Timangenso nsanja+ ndipo tipange makomo a zitseko ziwiriziwiri ndi mipiringidzo.+ Malo m’dzikoli akadalipo chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu.+ Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulira.”+ Chotero iwo anamangadi ndipo zinthu zinawayendera bwino.+

8 Asa anakhala ndi gulu lankhondo lonyamula zishango zazikulu+ ndi mikondo ing’onoing’ono,+ la asilikali 300,000 a fuko la Yuda.+ Analinso ndi asilikali onyamula zishango zazing’ono+ ndi odziwa kupinda uta okwanira 280,000+ a fuko la Benjamini. Onsewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima.

9 Pambuyo pake Zera Mwitiyopiya+ anabwera kudzamenyana nawo ali ndi gulu lankhondo la asilikali 1,000,000+ ndi magaleta 300, ndipo anafika ku Maresha.+ 10 Asa anapita kukamenyana naye ndipo iwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo m’chigwa cha Sefata ku Maresha. 11 Tsopano Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake,+ kuti: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera m’dzina lanu+ kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+

12 Atatero, Yehova anagonjetsa+ Aitiyopiyawo pamaso pa Asa ndi Ayuda, ndipo Aitiyopiyawo anayamba kuthawa. 13 Asa ndi anthu amene anali naye anawathamangitsa mpaka kukafika ku Gerari,+ ndipo Aitiyopiyawo anapitiriza kuphedwa mpaka palibe amene anatsala ndi moyo, popeza Yehova+ ndi gulu lake+ anawagonjetseratu. Pambuyo pake, anthuwo anatenga zofunkha zochuluka zedi.+ 14 Kuwonjezera apo, anawononga mizinda yonse yozungulira Gerari chifukwa mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira anthu a m’mizindayo. Iwo anafunkha mizinda yonseyo, chifukwa munali zambiri zoti afunkhe.+ 15 Anawononganso mahema+ a anthu okhala ndi ziweto n’kutengamo+ ziweto zambiri ndi ngamila.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

15 Tsopano mzimu+ wa Mulungu unafikira Azariya mwana wa Odedi.+ 2 Chotero iye anapita kukaonekera kwa Asa n’kumuuza kuti: “Tamverani mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.+ Mukamufunafuna+ iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.+ 3 Masiku ambiri Aisiraeli+ anakhala opanda Mulungu woona, opanda wansembe woti aziwaphunzitsa+ ndiponso opanda Chilamulo. 4 Koma iwo atabwerera kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli+ m’mavuto awowo+ n’kumufunafuna, iye analola kuti amupeze.+ 5 M’masiku amenewo, anthu sankayenda mwamtendere+ chifukwa panali zisokonezo zambiri pakati pa anthu onse okhala m’madera a m’dzikoli.+ 6 Anthuwo anagonjetsana chifukwa anaukirana okhaokha. Fuko limodzi linkamenyana ndi fuko lina+ ndiponso mzinda ndi mzinda wina, popeza Mulungu anawasiya pa chisokonezo ndi zowawa zosiyanasiyana.+ 7 Koma inuyo khalani olimba mtima+ ndipo musagwe ulesi,+ pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.”+

8 Asa atangomva mawu amenewa ndi ulosi wa mneneri Odedi,+ analimba mtima n’kuyamba kuchotsa zinthu zonyansa+ m’dziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi m’mizinda imene analanda m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Anayambanso kukonza guwa lansembe la Yehova limene linali patsogolo pa khonde la nyumba ya Yehova.+ 9 Atatero anayamba kusonkhanitsa pamodzi Ayuda ndi Abenjamini+ onse, ndi alendo ambirimbiri+ amene anali pakati pawo ochokera ku fuko la Efuraimu, Manase ndi Simiyoni. Alendowa anathawa ku Isiraeli n’kubwera kwa iye ataona kuti Yehova Mulungu wake ali naye.+ 10 Iwo anasonkhana ku Yerusalemu m’mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. 11 Kenako anapereka nsembe kwa Yehova pa tsiku limenelo kuchokera pa zofunkha zimene anabweretsa. Anapereka nsembe ng’ombe 700 ndi nkhosa 7,000. 12 Kuwonjezera apo, anachita pangano+ loti adzafunafuna Yehova Mulungu wa makolo awo ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse.+ 13 Komanso kuti aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli ayenera kuphedwa,+ kaya ndi wamng’ono kapena wamkulu,+ kaya ndi mwamuna kapena mkazi.+ 14 Choncho analumbira+ kwa Yehova ndi mawu okweza ndi kufuula mwachimwemwe, ndi kuliza malipenga ndi nyanga. 15 Ayuda onse anayamba kusangalala+ chifukwa cha zimene analumbirazo popeza analumbira ndi mtima wawo wonse, komanso chifukwa chakuti anafunafuna Mulungu mokondwa kwambiri moti iye analola kuti amupeze.+ Choncho Yehova anapitiriza kuwapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.+

16 Mfumu Asa+ inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika.+ Kenako Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera n’kukalitentha+ m’chigwa cha Kidironi.+ 17 Koma malo okwezeka+ analipobe mu Isiraeli.+ Ngakhale zinali choncho, mtima wa Asa unali wathunthu masiku ake onse.+ 18 Iye anabweretsa kunyumba ya Mulungu woona zinthu zimene bambo ake anaziyeretsa,+ komanso zinthu zimene iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide, ndi ziwiya zina.+ 19 Pa nthawiyo sipanachitike nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ulamuliro wa Asa.+

16 M’chaka cha 36 cha ulamuliro wa Asa, Basa+ mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda. Kenako anayamba kumanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama,+ kuti anthu asamapite kwa Asa mfumu ya Yuda kapena kubwera kuchokera kwa Asa.+ 2 Tsopano Asa anatenga siliva ndi golide pa chuma cha m’nyumba ya Yehova+ ndiponso cha m’nyumba ya mfumu,+ n’kuzitumiza kwa Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya+ amene anali kukhala ku Damasiko.+ Anam’tumiziranso mawu akuti: 3 “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Taona, ndakutumizira siliva ndi golide. Pita ukaphwanye pangano lako ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli kuti achoke kwa ine.”+

4 Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga Iyoni,+ Dani,+ Abele-maimu,+ ndi malo onse osungiramo zinthu+ a m’mizinda ya Nafitali.+ 5 Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama n’kuimitsa ntchito yake.+ 6 Ndiyeno mfumu Asa inatenga Ayuda onse,+ ndipo iwo anapita kukatenga miyala ya ku Rama+ ndi matabwa ake, zimene Basa ankamangira.+ Mfumuyo inatenga zinthu zimenezo n’kuyamba kukamangira Geba+ ndi Mizipa.+

7 Pa nthawi imeneyo, wamasomphenya* Haneni+ anapita kwa Asa mfumu ya Yuda n’kumuuza kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya,+ osadalira Yehova Mulungu wanu,+ gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu. 8 Kodi Aitiyopiya+ ndi Alibiya+ sanali gulu lankhondo lalikulu, la anthu ambiri, magaleta ambiri, ndi okwera pamahatchi ambirinso?+ Chifukwa chakuti munadalira Yehova, kodi iye sanawapereke m’manja mwanu?+ 9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+

10 Koma Asa anamukwiyira wamasomphenyayo. Kenako anamuika m’ndende n’kumumanga m’matangadza+ popeza anamupsera mtima kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.+ Pa nthawi yomweyo, Asa anayamba kuponderezanso+ anthu ake ena. 11 Nkhani zokhudza Asa, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.

12 M’chaka cha 39 cha ulamuliro wa Asa, iye anadwala nthenda ya mapazi+ mpaka matendawo anakula kwambiri. Koma ngakhale pamene anali kudwala, iye anafunafuna ochiritsa+ osati Yehova.+ 13 Pomalizira pake, Asa anamwalira m’chaka cha 41 cha ulamuliro wake ndipo anagona pamodzi ndi makolo ake.+ 14 Choncho anamuika m’manda ake olemekezeka kwambiri,+ amene iye anadzikumbira mu Mzinda wa Davide.+ Pomuika m’mandamo, anamugoneka pabedi pomwe anathirapo mafuta a basamu ambiri+ ndi msakanizo wapadera wa mafuta onunkhira.+ Kuwonjezera apo, pamaliro ake anapserezapo zofukiza+ zochuluka kwambiri.

17 Ndiyeno Yehosafati+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli. 2 Iye anaika magulu ankhondo m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Anamanganso midzi ya asilikali m’dziko la Yuda ndi m’mizinda ya Efuraimu imene Asa bambo ake analanda.+ 3 Yehova anapitiriza kukhala ndi Yehosafati+ chifukwa anayenda m’njira zimene Davide kholo lake+ anayenda kalekale, ndipo sanafunefune Abaala.+ 4 Iye anafunafuna Mulungu wa bambo ake+ ndipo anayenda+ motsatira chilamulo chake, sanatsatire zochita za Aisiraeli.+ 5 Yehova anachititsa kuti ufumuwo ukhazikike m’manja mwake+ ndipo Ayuda onse anapitiriza kupereka+ mphatso kwa Yehosafati. Chotero iye anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka.+ 6 Komanso analimba mtima potsatira njira+ za Yehova ndipo anachotsa m’dziko la Yuda malo okwezeka+ ndi mizati yopatulika.+

7 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, anaitana akalonga ake kuti aziphunzitsa m’mizinda ya Yuda. Akalongawo anali Beni-hayili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya, 8 pamodzi ndi Alevi. Aleviwo anali Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yehonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobi-adoniya, pamodzi ndi ansembe Elisama ndi Yehoramu.+ 9 Iwo anayamba kuphunzitsa+ mu Yuda pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.+ Ankayendayenda m’mizinda yonse ya Yuda n’kumaphunzitsa anthu.

10 Mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira maufumu onse a m’mayiko ozungulira Yuda, ndipo sanachite nkhondo ndi Yehosafati.+ 11 Afilisiti anali kubweretsa+ mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho.+ Aluya+ nawonso anali kum’bweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi mbuzi zamphongo 7,700.+

12 Zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino Yehosafati ndipo mphamvu zake zinapitiriza kukula kwambiri.+ Iye anayamba kumanga m’dziko la Yuda malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ ndiponso mizinda yosungirako zinthu.+ 13 Panali zinthu zambiri m’mizinda ya Yuda zimene zinakhala zake. Ku Yerusalemu anali ndi asilikali,+ amuna amphamvu+ ndi olimba mtima. 14 Awa ndiwo anali maudindo awo potsata nyumba ya makolo awo: Adinala anali mmodzi wa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 a fuko la Yuda. Iye anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 300,000.+ 15 Adinalayo ankayang’anira Yehohanani mkulu wa asilikali, yemwe anali ndi asilikali 280,000. 16 Iye ankayang’aniranso Amasiya mwana wa Zikiri, yemwe anadzipereka kutumikira+ Yehova. Amasiyayo anali ndi amuna amphamvu ndi olimba mtima okwana 200,000. 17 Kuchokera m’fuko la Benjamini+ panali Eliyada, mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima yemwe anali ndi asilikali 200,000 onyamula mauta ndi zishango.+ 18 Iye ankayang’anira Yehozabadi yemwe anali ndi asilikali 180,000 okonzekera kumenya nkhondo. 19 Amenewa ndiwo anali kutumikira mfumu, kuwonjezera pa anthu amene mfumuyo inawaika m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ m’dziko lonse la Yuda.

18 Yehosafati anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu,+ koma anachita mgwirizano wa ukwati+ ndi Ahabu.+ 2 Chotero patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ng’ombe zambiri n’kuzipereka nsembe+ m’malo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera+ Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+ 3 Ahabu mfumu ya Isiraeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti: “Kodi upita nane ku Ramoti-giliyadi?”+ Yehosafati anamuyankha kuti: “Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu ako ndi amodzi, ndipo ali nawe limodzi pankhondoyi.”+

4 Komabe Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, umve+ kaye mawu a Yehova.” 5 Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri+ pamodzi. Analipo amuna 400, ndipo inawafunsa kuti: “Kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?”+ Iwo anayankha kuti: “Pitani, ndipo Mulungu woona akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”

6 Koma Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene watsala?+ Ngati alipo, tiyeni tifunse kudzera mwa ameneyo.”+ 7 Poyankha, mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati+ kuti: “Pali munthu mmodzi+ amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye, koma ineyo ndimadana naye+ kwambiri, chifukwa masiku ake onse salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Munthuyo dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.”+ Koma Yehosafati anati: “Musalankhule choncho mfumu.”+

8 Chotero mfumu ya Isiraeli inaitana nduna ya panyumba ya mfumu,+ n’kuiuza kuti: “Kaitane Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye msangamsanga.”+ 9 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anali atakhala pabwalo* la pachipata cha Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu, atavala zovala zachifumu.+ Aneneri onse anali pamaso pawo ndipo anali kulosera.+ 10 Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga+ zachitsulo n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Ndi nyanga izi mudzakankha Asiriya mpaka kuwatha.’”+ 11 Aneneri ena onse analinso kulosera zofanana ndi zomwezo, ndipo anali kunena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana.+ Yehova akaperekadi mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+

12 Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Tamvera, mawu amene aneneri onse alankhula kwa mfumu ndi abwino. Nawenso mawu ako akakhale ngati mawu awo,+ ndipo ukalankhule zabwino.”+ 13 Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Mulungu wanga anene n’zimene ndikalankhule.”+ 14 Kenako anafika kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana. Iwo akaperekedwa m’manja mwanu.”+ 15 Ndiyeno mfumuyo inamuuza kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati+ kuti uzilankhula kwa ine zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?”+ 16 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+

17 Mfumu ya Isiraeli itamva zimenezi inauza Yehosafati kuti: “Pajatu ndinakuuza kuti, ‘Adzalosera zoipa zokhudza ine, osati zabwino.’”+

18 Mikaya anapitiriza kunena kuti: “Choncho imvani mawu a Yehova:+ Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu,+ makamu onse+ akumwamba ataimirira kudzanja lake lamanja ndi kumanzere kwake.+ 19 Kenako Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti apite ku Ramoti-giliyadi n’kukafa?’ Choncho panali kukambirana. Uyu anali kunena zakutizakuti, uyunso n’kumanena zakutizakuti.+ 20 Pomalizira pake, mzimu+ wina unabwera kudzaima pamaso pa Yehova n’kunena kuti, ‘Ine ndikam’pusitsa.’ Ndipo Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukam’pusitsa motani?’+ 21 Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukam’pusitsadi ndipo zikakuyendera bwino.+ Pita kachite momwemo.’+ 22 Choncho Yehova waika mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anuwa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+

23 Tsopano Zedekiya+ mwana wa Kenaana+ anayandikira Mikaya+ ndipo anam’menya mbama.+ Kenako anati: “Kodi mzimu wa Yehova wachoka bwanji kwa ine n’kukalankhula ndi iwe?”+ 24 Pamenepo Mikaya anati: “Udzadziwa zimenezo tsiku+ limene udzalowe m’chipinda chamkati kukabisala.”+ 25 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Tengani Mikaya mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu.+ 26 Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Kam’tsekereni munthu uyu.+ Muzim’patsa chakudya chochepa+ ndi madzinso ochepa, kufikira ine nditabwerera mu mtendere.”’”+ 27 Pamenepo Mikaya ananena kuti: “Mukakabwereradi mu mtendere, ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Anatinso: “Imvani anthu nonsenu.”+

28 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 29 Tsopano mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha+ kuti ndisadziwike, ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma iweyo uvale zovala zako zachifumu.”+ Chotero mfumu ya Isiraeli inadzisintha, kenako iwo anayamba kumenya nawo nkhondo.+ 30 Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu ake oyang’anira asilikali okwera magaleta, kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamng’ono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.”+ 31 Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Iyi ndiyo mfumu ya Isiraeli.”+ Choncho anatembenuka kuti amenyane naye, koma Yehosafati anayamba kukuwa popempha thandizo,+ ndipo Yehova anamuthandiza.+ Nthawi yomweyo Mulungu anawachititsa kuchoka kwa iye.+ 32 Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, nthawi yomweyo anasiya kumuthamangitsa ndipo anabwerera.+

33 Ndiyeno munthu wina anakoka uta n’kuponya muvi wake chiponyeponye, koma analasa+ mfumu ya Isiraeli pampata umene unali pakati pa chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo, ndi zovala zake zina zodzitetezera. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti:+ “Tembenuza galetali ndipo unditulutse m’bwalo lankhondoli, chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 34 Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo, ndipo mfumu ya Isiraeliyo anaiimiritsa m’galeta moyang’anizana ndi Asiriya mpaka madzulo. Potsirizira pake mfumuyo inafa pamene dzuwa linali kulowa.+

19 Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera mu mtendere+ kunyumba kwake ku Yerusalemu. 2 Tsopano Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya,+ anapita kukaonekera kwa Mfumu Yehosafati ndipo anaifunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa+ kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana+ ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.+ 3 Komabe, pali zinthu zabwino+ zimene zapezeka mwa inu, chifukwa mwachotsa mizati yopatulika m’dzikoli,+ ndipo mwakonza mtima wanu kuti mufunefune Mulungu woona.”+

4 Yehosafati anapitiriza kukhala ku Yerusalemu. Iye anayambanso kupita pakati pa anthu, kuyambira ku Beere-seba+ mpaka kudera lamapiri la Efuraimu,+ kuti awabwezere kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.+ 5 Anaika oweruza m’dziko lonselo, mumzinda ndi mzinda, m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 6 Ndiyeno anauza oweruzawo kuti: “Samalani zochita zanu+ chifukwa simukuweruzira munthu koma mukuweruzira Yehova,+ ndipo iye ali nanu pa ntchito yoweruzayi.+ 7 Tsopano mantha+ a Yehova akugwireni.+ Samalani mmene mukuchitira+ chifukwa Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo+ kapena watsankho,+ ndipo salandira chiphuphu.”+

8 Ku Yerusalemu nakonso Yehosafati anaikako Alevi ena,+ ansembe,+ ndi ena mwa atsogoleri a nyumba za makolo+ a Isiraeli, kuti azionetsetsa kuti anthu akutsatira chilamulo+ cha Yehova ndi kuti aziweruza milandu+ ya anthu a ku Yerusalemu. 9 Kuwonjezera apo, anawalamula kuti: “Muzichita zimenezi moopa+ Yehova ndi mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu. 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene akukhala m’mizinda yawo, wokhudza kukhetsa magazi,+ chilamulo,+ ndi zigamulo,+ muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti mkwiyo wa Mulungu+ ungakuyakireni inuyo ndi abale anu. Muzichita zimenezi n’cholinga choti musapalamule mlandu. 11 Ndakupatsani wansembe wamkulu Amariya kuti azisamalira nkhani iliyonse yokhudza Yehova.+ Zebadiya mwana wa Isimaeli mtsogoleri wa nyumba ya Yuda aziyang’anira nkhani iliyonse yokhudza mfumu. Ndakupatsaninso Alevi kuti akhale oyang’anira anu. Khalani olimba mtima+ ndipo gwirani ntchitoyi. Yehova+ adalitse zabwino zimene muzichita.”+

20 Pambuyo pake ana a Mowabu,+ ana a Amoni,+ pamodzi ndi Aamonimu+ ena, anabwera kudzamenyana ndi Yehosafati.+ 2 Choncho anthu anapita kukamuuza Yehosafati kuti: “Kwabwera khamu lalikulu la anthu ochokera kuchigawo cha kunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu. Panopa iwo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+ 3 Yehosafati atamva zimenezi anachita mantha+ ndipo anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.+ Choncho analengeza kuti Ayuda onse asale kudya.+ 4 Ndiyeno Ayudawo anasonkhana pamodzi kuti afunsire kwa Yehova.+ Iwo anachokera m’mizinda yonse ya Yuda n’kubwera kudzafunsira kwa Yehova.+

5 Kenako Yehosafati anaimirira pakati pa mpingo wa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, m’nyumba ya Yehova+ patsogolo pa bwalo latsopano,+ 6 n’kunena kuti:+

“Inu Yehova Mulungu wa makolo athu,+ kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Kodi m’dzanja lanu si muli mphamvu kotero kuti palibe amene angalimbane nanu?+ 7 Kodi inuyo Mulungu wathu+ si paja munathamangitsa anthu amene anali kukhala m’dziko lino pamaso pa anthu anu Aisiraeli,+ n’kulipereka+ kwa mbewu ya Abulahamu yemwe anali kukukondani,+ kuti likhale lawo mpaka kalekale? 8 Ndiyeno iwo anayamba kukhalamo ndipo anakumangirani malo opatulika a dzina lanu m’dzikolo,+ n’kunena kuti, 9 ‘Likatigwera tsoka,+ lupanga, chiweruzo chowawa, mliri+ kapena njala,+ tiziima pamaso pa nyumba iyi+ ndi pamaso panu (popeza dzina lanu+ lili m’nyumba iyi), kuti tifuulire inu kuti mutithandize m’masautso athu, ndipo inu muzimva ndi kutipulumutsa.’+ 10 Tsopano taonani zimene akuchita ana a Amoni,+ ana a Mowabu+ ndi a kudera lamapiri la Seiri.+ Inu simunalole kuti Aisiraeli alowe m’dziko lawo pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo ndipo anawasiya osawawononga.+ 11 Tsopano akutilipira+ mwa kubwera kudzatithamangitsa m’cholowa chanu chimene munatipatsa.+ 12 Inu Mulungu wathu kodi simuwaweruza?+ Ifeyo patokha tilibe mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu limene likubwera kudzamenyana nafeli+ ndipo sitikudziwa chochita,+ koma maso athu ali pa inu.”+

13 Nthawi yonseyi anthu onse a ku Yuda anali ataimirira pamaso pa Yehova,+ kuphatikizapo akazi awo ndi ana awo, ngakhalenso ana awo ang’onoang’ono.+

14 Tsopano mzimu+ wa Yehova unafikira Yahazieli yemwe anali pakati pa mpingowo. Iye anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Benaya, Benaya anali mwana wa Yeyeli, Yeyeli anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali Mlevi, mmodzi wa ana a Asafu.+ 15 Choncho Yahazieli anati: “Tamverani Ayuda nonsenu, anthu okhala mu Yerusalemu, ndi inu Mfumu Yehosafati! Izi n’zimene Yehova wanena kwa inu, ‘Musaope+ kapena kuchita mantha ndi khamu lalikululi, popeza nkhondoyi si yanu ndi ya Mulungu.+ 16 Mawa mupite kukakumana nawo. Iwo akubwera ndipo adzera pampata wa Zizi. Mukawapeza kumapeto kwa chigwa chimene chili kutsogolo kwa chipululu cha Yerueli. 17 Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo.+ Khalani m’malo anu, imani chilili+ ndi kuona Yehova akukupulumutsani.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+

18 Nthawi yomweyo Yehosafati anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo Ayuda onse ndi anthu okhala mu Yerusalemu anawerama pamaso pa Yehova kuti alambire Yehovayo.+ 19 Kenako Alevi+ omwe anali ana a Kohati+ ndi ana a Kora+ anaimirira ndi kutamanda Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mawu okweza kwambiri.+

20 Anthuwo ananyamuka m’mawa kwambiri n’kupita kuchipululu+ cha Tekowa.+ Ali m’njira, Yehosafati anaimirira n’kunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu!+ Khulupirirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mukhalitse. Khulupirirani aneneri+ ake kuti zinthu zikuyendereni bwino.”

21 Kenako iye anakambirana+ ndi anthuwo, n’kutenga anthu oimbira+ Yehova ndi omutamanda+ ovala zovala zokongola ndi zopatulika+ n’kuwaika patsogolo pa amuna onyamula zida.+ Iwo anali kunena kuti: “Tamandani Yehova,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+

22 Pa nthawi imene iwo ananyamuka akufuula mosangalala ndi kutamanda Mulungu, Yehova anaika amuna omwe anabisalira+ ana a Amoni, ana a Mowabu ndi a kudera lamapiri la Seiri omwe anali kupita ku Yuda, ndipo iwo anaphana okhaokha.+ 23 Ana a Amoni ndi ana a Mowabu anaukira anthu okhala kudera lamapiri la Seiri+ ndipo anawapha ndi kuwamaliza. Atatha kupha anthu a ku Seiri, iwo anaphana okhaokha.+

24 Kenako Ayuda anafika pansanja ya mlonda ya m’chipululu.+ Iwo atatembenuka kuti ayang’ane khamu lija, anangoona mitembo yokhayokha ili pansi+ popanda wopulumuka. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha+ zinthu zimene adaniwo anali nazo. Iwo anapeza zinthu zochuluka pakati pa anthuwo monga katundu wosiyanasiyana, zovala ndi zinthu zina zabwinozabwino. Chotero anayamba kutenga zinthuzo mpaka zinawakanika kunyamula.+ Kwa masiku atatu anakhala akututa zofunkhazo chifukwa zinalipo zambiri. 26 Pa tsiku lachinayi anasonkhana pachigwa cha Beraka ndipo kumeneko anatamanda Yehova.+ N’chifukwa chake malowo anawatcha dzina+ lakuti chigwa cha Beraka* mpaka lero.

27 Kenako Ayuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu, Yehosafati ali patsogolo pawo. Iwo anali akusangalala chifukwa Yehova anawathandiza kugonjetsa adani awo.+ 28 Choncho anafika ku Yerusalemu kunyumba ya Yehova+ akuimba ndi zoimbira za zingwe,+ azeze+ ndi malipenga.+ 29 Mantha+ ochokera kwa Mulungu anagwira mafumu onse a m’dzikolo atamva kuti Yehova wagonjetsa adani a Isiraeli.+ 30 Chotero ufumu wa Yehosafati unalibe chosokoneza chilichonse, ndipo Mulungu wake anapitiriza kumupatsa mpumulo pakati pa adani ake onse omuzungulira.+

31 Yehosafati+ anapitiriza kulamulira ku Yuda. Iye anali ndi zaka 35 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba+ mwana wa Sili. 32 Yehosafati anapitiriza kuyenda m’njira za Asa+ bambo ake. Sanapatuke panjirazo, ndipo anachita zoyenera pamaso pa Yehova.+ 33 Koma sanachotse malo okwezeka+ ndiponso anthuwo anali asanakonze mitima yawo kuti atsatire Mulungu wa makolo awo.+

34 Nkhani zina zokhudza Yehosafati, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’mawu a Yehu+ mwana wa Haneni.+ Mawuwa analembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli. 35 Pambuyo pa zimenezi, Yehosafati mfumu ya Yuda anachita mgwirizano ndi Ahaziya+ mfumu ya Isiraeli amene anachita zoipa.+ 36 Chotero anayamba kugwira naye limodzi ntchito yopanga zombo zopita ku Tarisi.+ Zombozo anazipangira ku Ezioni-geberi.+ 37 Koma Eliezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa analankhula mwaulosi motsutsana ndi Yehosafati, kuti: “Popeza mwachita mgwirizano ndi Ahaziya,+ Yehova awononga ntchito zanu.”+ Chotero zombozo zinasweka+ ndipo sizinathenso kupita ku Tarisi.+

21 Pomalizira pake, Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake+ mu Mzinda wa Davide. Kenako Yehoramu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 2 Yehoramu anali ndi abale ake, ana a Yehosafati. Abale akewo anali Azariya, Yehiela, Zekariya, Azariya, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Isiraeli. 3 Bambo awo anawapatsa mphatso zambiri+ zasiliva, zagolide, zinthu zina zabwinozabwino, ndi mizinda ya ku Yuda+ yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Koma ufumu anaupereka kwa Yehoramu+ chifukwa ndiye anali woyamba kubadwa.+

4 Yehoramu atayamba kulamulira mu ufumu wa bambo ake, iye analimbitsa ufumu wake. Chotero anapha abale ake+ onse ndi lupanga ndiponso akalonga ena a Isiraeli. 5 Yehoramu anayamba kulamulira ali ndi zaka 32, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.+ 6 Iye anayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ monga mmene ankachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 7 Koma Yehova sanafune kuwononga nyumba ya Davide+ chifukwa cha pangano+ limene anapangana ndi Davide, monga momwe anamuuzira kuti adzam’patsa+ nyale nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.+

8 M’masiku a Yehoramu, Aedomu+ anagalukira Yuda.+ Iwo anachoka m’manja mwa Yuda n’kusankha mfumu yoti iziwalamulira.+ 9 Choncho Yehoramu ndi akuluakulu a asilikali ake anapita kumeneko pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku n’kukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta. 10 Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Inalinso nthawi imeneyi pamene Libina+ anagalukira Yuda ndi kuchoka m’manja mwa Yehoramu chifukwa iye anali atasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.+ 11 Komanso iye anamanga malo okwezeka+ m’mapiri a ku Yuda kuti achititse anthu okhala mu Yerusalemu kuchita zoipa,+ ndiponso kuti asocheretse Yuda.+

12 Kenako anam’bweretsera kalata+ yochokera kwa mneneri Eliya.+ Kalatayo inati: “Yehova Mulungu wa Davide kholo lanu wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti sunayende m’njira za Yehosafati+ bambo ako, kapena m’njira za Asa+ mfumu ya Yuda, 13 koma wayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ n’kuchititsa Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuchita zoipa,+ monga mmene a m’nyumba ya Ahabu anachititsira ena kuchita zoipa,+ ndiponso wapha ngakhale abale ako a m’nyumba ya bambo ako amene anali abwino kuposa iwe,+ 14 tamvera tsopano! Yehova adzalanga mwamphamvu+ anthu ako,+ ana ako+ ndi akazi ako, ndipo adzawononga katundu wako yense. 15 Iweyo udzakhala wodwaladwala+ popeza udzadwala matenda a m’matumbo, mpaka matumbo ako adzatuluka chifukwa chodwala tsiku ndi tsiku.’”+

16 Chotero Yehova anachititsa Afilisiti+ ndi Aluya+ amene anali pafupi ndi Aitiyopiya+ kuukira Yehoramu.+ 17 Choncho iwo anabwera kudzalimbana nawo mpaka analowa mu Yuda. Anthuwo anatenga katundu yense amene anali m’nyumba ya mfumu,+ ana ake ndi akazi ake.+ Sanamusiyire mwana aliyense kupatulapo Yehoahazi+ mwana wake wamng’ono kwambiri. 18 Pambuyo pa zonsezi, Yehova anamudwalitsa matenda a m’matumbo osachiritsika.+ 19 Patatha zaka ziwiri zathunthu iye akudwala, matumbo ake+ anatuluka ndipo anamwalira ndi matenda oipawa. Anthu ake sanamupserezere zofukiza pa maliro ake ngati mmene anachitira+ pa maliro a makolo ake. 20 Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Pomalizira pake iye anapita popanda womumvera chisoni.+ Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide,+ koma osati m’manda a mafumu.+

22 Kenako anthu okhala mu Yerusalemu analonga ufumu Ahaziya*+ mwana wake wamng’ono kwambiri, kukhala mfumu m’malo mwake (chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya+ kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu).+ Tsopano Ahaziya mwana wa Yehoramu anayamba kulamulira monga mfumu ya Yuda. 2 Iye anayamba kulamulira+ ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri.+

3 Ahaziya nayenso anayenda m’njira za anthu a m’nyumba ya Ahabu+ chifukwa amayi ake+ ndi amene anali kumulangiza kuti azichita zoipa. 4 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova monga anachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa iwowo anakhala alangizi+ ake pambuyo pa imfa ya bambo ake, ndipo anam’pweteketsa. 5 Anatsatira malangizo+ awo ndipo anapita kunkhondo ndi Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Kumeneko oponya mivi analasa Yehoramu.+ 6 Choncho Yehoramu anabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti akachire zilonda zimene anam’vulaza ku Rama,+ pamene anali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.

Chotero Azariya*+ mwana wa Yehoramu+ mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu+ mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.+ 7 Koma Mulungu ndi amene anachititsa+ kuti Ahaziya awonongeke+ mwa kupita kwa Yehoramu. Atafika kumeneko, anatengana+ ndi Yehoramu n’kupita kukakumana ndi Yehu+ mdzukulu wa Nimusi,+ yemwe Yehova anam’dzoza+ kuti aphe a m’nyumba ya Ahabu.+ 8 Yehu atangoyamba kulimbana ndi a m’nyumba ya Ahabu,+ anapeza akalonga a Yuda ndi ana a abale ake a Ahaziya,+ omwe anali atumiki a Ahaziya, ndipo anawapha.+ 9 Kenako iye anayamba kufunafuna Ahaziya ndipo anthu anam’gwira+ akubisala ku Samariya+ n’kupita naye kwa Yehu. Atatero iwo anamupha n’kumuika m’manda+ popeza anati: “Iye ndi mdzukulu wa Yehosafati,+ yemwe anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”+ Tsopano panalibe aliyense wa m’nyumba ya Ahaziya amene akanatha kulamulira ufumuwo.

10 Kenako Ataliya,+ mayi wa Ahaziya ataona kuti mwana wake wafa, anapha ana onse achifumu a nyumba ya Yuda.+ 11 Koma Yehosabati+ mwana wamkazi wa mfumu, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa m’chipinda chamkati chogona. Yehosabati, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu,+ mkazi wa wansembe Yehoyada,+ (popeza iye anali mlongo wake wa Ahaziya,) anabisa mwanayo chifukwa choopa Ataliya, ndipo mwanayo sanaphedwe.+ 12 Anapitiriza kubisidwa m’nyumba ya Mulungu woona zaka 6,+ pamene Ataliya+ anali mfumukazi ya dzikolo.+

23 M’chaka cha 7, Yehoyada+ analimba mtima n’kuitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ ndipo anachita nawo pangano. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yerohamu, Isimaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. 2 Pambuyo pake, iwo anayendayenda m’dziko lonse la Yuda n’kusonkhanitsa Alevi+ kuchokera m’mizinda yonse ya Yuda ndi atsogoleri+ a nyumba za makolo+ a Isiraeli. Atatero anapita ku Yerusalemu. 3 Kenako mpingo wonsewo unachita pangano+ ndi mfumu m’nyumba+ ya Mulungu woona. Ndiyeno Yehoyada anawauza kuti:

“Mwana wa mfumu+ ayenera kulamulira,+ monga momwe Yehova analonjezera ponena za ana a Davide.+ 4 Ndiyeno muchite izi: Gawo limodzi mwa magawo atatu a ansembe+ ndi Alevi+ amene ali pakati panu omwe adzabwere pa sabata,+ lidzakhale alonda a pamakomo.+ 5 Gawo limodzi mwa magawo atatu lidzakhale panyumba ya mfumu,+ ndipo gawo lina limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata chotchedwa Maziko.+ Anthu onse adzakhale pamabwalo+ a nyumba ya Yehova. 6 Musadzalole kuti aliyense alowe m’nyumba ya Yehova+ kupatulapo ansembe ndi Alevi amene azidzatumikira.+ Amenewa ndi amene adzalowe chifukwa ndi gulu loyera+ ndipo anthu onse adzakwaniritsa udindo wawo kwa Yehova mwa kukhala panja. 7 Alevi adzazungulire mfumuyo kumbali zonse,+ aliyense atatenga zida zake m’manja, ndipo aliyense wolowa m’nyumbayo adzaphedwe. Muzidzakhala limodzi ndi mfumuyo ikamalowa ndiponso ikamatuluka.”

8 Alevi ndi Ayuda onse anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada+ analamula.+ Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata, limodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata,+ popeza wansembe Yehoyada anali asanawauze+ kuti azipita. 9 Kuwonjezera apo, wansembe Yehoyada anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja+ mikondo, zishango ndi zishango zozungulira+ zimene zinali za Mfumu Davide,+ zomwe zinali m’nyumba ya Mulungu woona.+ 10 Iye anauza anthu onse kuti aimirire,+ kuyambira kumbali yakumanja ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere ya nyumbayo. Anaimiriranso pafupi ndi guwa lansembe ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anthuwo anazungulira mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga chida chake m’manja. 11 Kenako anatulutsa mwana wa mfumu uja.+ Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu, ndipo Yehoyada ndi ana ake anamudzoza+ n’kuyamba kunena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+

12 Ataliya atamva anthu akuchita phokoso komanso akuthamanga ndi kutamanda mfumu,+ nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova. 13 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala chake+ pakhomo. Anaonanso akalonga+ ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba+ malipenga. Panalinso oimba+ ndi zipangizo zoimbira ndiponso anthu otsogolera poimba nyimbo zotamanda. Nthawi yomweyo Ataliya anang’amba zovala zake n’kuyamba kunena kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+ 14 Koma wansembe Yehoyada anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa, n’kuwauza kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu!+ Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!” Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Musam’phere panyumba ya Yehova.” 15 Choncho anam’gwira n’kutuluka naye. Atangofika pakhomo la kunyumba ya mfumu lolowera mahatchi, anam’phera pomwepo.+

16 Kenako Yehoyada anachita pangano pakati pa iyeyo, anthu onse, ndi mfumu kuti anthuwo apitiriza kukhala anthu+ a Yehova. 17 Pambuyo pake, anthu onse anapita kukachisi wa Baala n’kukamugwetsa+ ndipo anagwetsanso maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha+ patsogolo pa maguwa ansembewo. 18 Kuwonjezera apo, Yehoyada anapereka ntchito za panyumba ya Yehova kwa ansembe ndi Alevi amene Davide+ anawaika m’magulu panyumba ya Yehova, kuti azipereka nsembe zopsereza za Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Anawauza kuti azizipereka mosangalala poimba nyimbo motsatira ndondomeko imene Davide anakhazikitsa. 19 Choncho anaika alonda a pazipata+ pafupi ndi zipata+ za nyumba ya Yehova kuti aliyense wodetsedwa mwa njira ina iliyonse asalowe. 20 Atatero anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ anthu olemekezeka, atsogoleri a anthuwo, ndi anthu onse a m’dzikolo, n’kutsetsereka nayo mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova.+ Anthuwo anadzera pachipata chakumtunda n’kukafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo anaikhazika pampando wachifumu+ wa ufumuwo. 21 Anthu onse a m’dzikolo anapitiriza kusangalala,+ ndipo mumzindawo munali bata. Ataliya anali atamupha ndi lupanga.+

24 Yehoasi anali ndi zaka 7 pamene anayamba kulamulira.+ Iye analamulira zaka 40 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Beere-seba+ ndipo dzina lawo linali Zibiya. 2 Yehoasi+ anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ masiku onse a wansembe Yehoyada.+ 3 Yehoyada anapezera Yehoasi akazi awiri, choncho iye anabereka ana aamuna ndi aakazi.+

4 Pambuyo pake Yehoasi anafunitsitsa mumtima mwake kukonzanso nyumba ya Yehova.+ 5 Chotero anasonkhanitsa ansembe+ ndi Alevi n’kuwauza kuti: “Pitani m’mizinda ya Yuda kukasonkhanitsa ndalama kwa Aisiraeli onse kuti muzikonzera+ nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka.+ Chitani zimenezi mwachangu.” Koma Aleviwo sanachite zimenezo mwachangu.+ 6 Ndiyeno mfumuyo inaitana mtsogoleri wawo Yehoyada n’kumufunsa kuti:+ “Bwanji simunafunse Alevi kuti afotokoze za nkhani yobweretsa msonkho wopatulika kuchokera kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu? Si paja anayenera kubweretsa msonkho umene Mose+ mtumiki wa Yehova analamula, msonkho wopatulika wa mpingo wa Isiraeli wogwiritsa ntchito pachihema cha Umboni?+ 7 Pajatu ana+ a Ataliya mkazi woipa uja anathyola nyumba ya Mulungu woona,+ n’kutenga zinthu zonse zopatulika+ za m’nyumba ya Yehovayo n’kukazipereka kwa Abaala.”+ 8 Tsopano mfumuyo inawauza zochita ndipo anapanga bokosi+ n’kuliika panja, pachipata cha nyumba ya Yehova. 9 Atatero anauza anthu onse a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho wopatulika+ umene Mose+ mtumiki wa Mulungu woona analamula Aisiraeli m’chipululu. 10 Akalonga onse+ ndi anthu onse anayamba kusangalala,+ ndipo anali kubweretsa ndalama za msonkhowo n’kumaziponya m’bokosi+ lija kufikira aliyense anapereka.

11 Pa nthawi yoyenera, Alevi+ ankanyamula bokosilo n’kupita nalo kwa mfumu. Iwo akangoona kuti muli ndalama zambiri,+ mlembi+ wa mfumu ndi mtumiki wa wansembe wamkulu ankabwera n’kukhuthula ndalama zimene zinali m’bokosilo, n’kulinyamula kukalibwezeretsa pamalo ake. Ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku moti anasonkhetsa ndalama zambiri. 12 Mfumuyo ndi Yehoyada ankapereka ndalamazo kwa anthu ogwira ntchito+ yokonza nyumba ya Yehova.+ Iwowo analemba ntchito anthu osema miyala+ ndi amisiri+ okonza nyumba ya Yehova.+ Analembanso ntchito amisiri a mkuwa ndi a zitsulo oti akonze nyumba ya Yehova.+ 13 Anthu ogwira ntchitowo anayamba ntchito yawo+ ndipo ntchito yokonza nyumbayo inali kuyenda bwino. Pomaliza pake anakonza nyumba ya Mulungu woona kuti ikhale mmene inayenera kukhalira ndipo anailimbitsa. 14 Atangomaliza ntchitoyo anabweretsa ndalama zotsalazo kwa mfumu ndi Yehoyada. Ndi ndalamazo, iwo anapanga ziwiya za nyumba ya Yehova ndiponso ziwiya zogwiritsira ntchito pa utumiki+ ndi popereka zopereka. Anapanganso makapu+ ndi ziwiya zagolide+ ndi siliva, ndipo nsembe zopsereza+ zinayamba kuperekedwa nthawi zonse m’nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

15 Yehoyada anakalamba atakhutira ndi moyo wake wa zaka zambiri,+ ndipo anamwalira ali ndi zaka 130. 16 Choncho anamuika m’manda a mafumu mu Mzinda wa Davide,+ chifukwa anachita zabwino mu Isiraeli+ ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.

17 Yehoyada atamwalira, akalonga+ a Yuda anabwera n’kudzagwada pamaso pa mfumu ndipo mfumuyo inawamvera.+ 18 M’kupita kwa nthawi iwo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo awo n’kuyamba kutumikira mizati yopatulika+ ndiponso mafano.+ Chotero mkwiyo wa Mulungu unagwera Yuda ndi Yerusalemu chifukwa cha kupalamula kwawoko.+ 19 Yehova anapitiriza kutumiza aneneri+ pakati pawo kuti awabwezere kwa iye. Aneneriwo anapitiriza kupereka umboni wowatsutsa, koma sanamvere.+

20 Tsopano mzimu wa Mulungu+ unadzaza+ Zekariya+ mwana wa wansembe Yehoyada+ ndipo anaimirira pamalo okwera, n’kuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Kodi simukuona kuti zinthu sizikukuyenderani bwino?+ Popeza mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+ 21 Pamapeto pake anthuwo anam’konzera chiwembu+ ndipo anam’ponya miyala+ pabwalo la nyumba ya Yehova, atalamulidwa ndi mfumu. 22 Mfumu Yehoasi sanakumbukire kukoma mtima kosatha kumene Yehoyada bambo a Zekariya anamusonyeza,+ ndipo anapha mwana wawo yemwe pakufa ananena kuti: “Yehova aone zimene mwachitazi ndi kubwezera.”+

23 Kumayambiriro+ kwa chaka chotsatira, gulu lankhondo la ku Siriya+ linabwera kudzamenyana naye,+ ndipo linalowa mu Yuda ndi Yerusalemu. Asilikaliwo anachotsa akalonga onse+ pakati pa anthuwo n’kuwapha, ndipo zinthu zonse zimene anafunkha anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko.+ 24 Gulu lankhondo la Siriyalo linalowa m’dzikolo ndi amuna ochepa,+ koma Yehova anapereka m’manja mwawo gulu lankhondo lalikulu kwambiri+ popeza iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo. Asiriyawo anaperekanso chiweruzo kwa Yehoasi.+ 25 Asilikaliwo atachoka (popeza anamusiya akuvutika kwambiri),+ atumiki ake anam’konzera chiwembu+ chifukwa cha magazi+ a ana a wansembe Yehoyada+ ndipo anamuphera pabedi+ lake. Kenako anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike m’manda a mafumu.+

26 Amene anam’konzera chiwembucho ndi awa: Zabadi+ yemwe mayi ake anali Simeyati Muamoni ndi Yehozabadi yemwe mayi ake anali Simiriti Mmowabu. 27 Nkhani zokhudza ana ake, mauthenga ochuluka omutsutsa,+ ndi ntchito yokonzanso maziko+ a nyumba ya Mulungu woona, zinalembedwa m’ndemanga za Buku+ la Mafumu. Kenako Amaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

25 Amaziya+ anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadana.+ 2 Amaziya anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova,+ koma osati ndi mtima wathunthu.+ 3 Ndiyeno ufumuwo utangolimba m’manja mwake, iye anapha+ atumiki ake+ amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+ 4 Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha m’buku la Mose,+ chimene Yehova analamula kuti: “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana,+ ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+

5 Kenako Amaziya anasonkhanitsa Ayuda n’kuwaimiritsa motsatira nyumba ya makolo awo.+ Anawaika m’magulu a anthu 1,000+ ndi mtsogoleri wawo, ndiponso m’magulu a anthu 100+ ndi mtsogoleri wawo, a mafuko a Yuda ndi Benjamini. Iye anawalemba mayina anthuwo, kuyambira azaka 20+ kupita m’tsogolo ndipo anapeza kuti analipo 300,000. Anali amuna ochita kusankhidwa a m’gulu la asilikali, onyamula mkondo waung’ono+ ndi chishango chachikulu.+ 6 Kuwonjezera apo, analemba ganyu amuna amphamvu ndi olimba mtima a ku Isiraeli okwanira 100,000, pamtengo wa matalente a siliva* 100. 7 Ndiyeno munthu winawake wa Mulungu woona+ anapita kwa Amaziya n’kumuuza kuti: “Inu mfumu, musalole kuti gulu lankhondo la Isiraeli lipite nanu limodzi, chifukwa Yehova sali ndi Aisiraeli,+ kutanthauza ana onse a Efuraimu. 8 Inuyo mupite nokha ndipo limbani mtima kukamenya nkhondo.+ Mulungu woona angakuchititseni kugonja kwa adani anu, chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu zomuthandiza+ munthu kapena zom’chititsa kugonja.”+ 9 Pamenepo Amaziya+ anafunsa munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Nanga bwanji za matalente 100 amene ndapereka kwa asilikali a ku Isiraeli aja?”+ Munthu wa Mulungu woonayo anayankha kuti: “Yehova akhoza kukupatsani zambiri kuposa pamenepa.”+ 10 Chotero Amaziya anapatula asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efuraimu n’kuwauza kuti abwerere kwawo. Koma asilikaliwo anawakwiyira kwambiri Ayuda moti anabwerera kwawo ali okwiya kwambiri.+

11 Ndiyeno Amaziya analimba mtima n’kutsogolera anthu ake kupita kuchigwa cha Mchere.+ Kumeneko anapha ana a Seiri+ okwana 10,000.+ 12 Panalinso anthu 10,000 amene ana a Yuda anawagwira amoyo. Choncho anapita nawo pathanthwe lomwe linali pamwamba kwambiri n’kuyamba kuwaponya kuchokera pathanthwepo ndipo onsewo anaphulikaphulika.+ 13 Asilikali amene Amaziya anawabweza kuti asapite naye limodzi kunkhondo aja,+ anayamba kuukira mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya+ mpaka ku Beti-horoni,+ ndipo anapha anthu 3,000 a m’mizindayo ndi kufunkha zinthu zambiri.

14 Koma pobwerera kuchokera kokapha Aedomu, Amaziya anatenga milungu+ ya ana a Seiri n’kukaiimika kuti ikhale milungu yake.+ Kenako anayamba kuigwadira+ ndi kuifukizira nsembe yautsi.+ 15 Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya ndipo anatumiza mneneri kukam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mwafunafuna+ milungu+ yomwe sinapulumutse anthu awo m’manja mwanu?”+ 16 Mneneriyo atangonena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Siya kunena zimenezi.+ Kodi ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndithu ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kuti akuwonongeni+ chifukwa cha zimene mwachitazi,+ ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+

17 Tsopano Amaziya mfumu ya Yuda anakambirana ndi anthu ena n’kutumiza uthenga kwa Yehoasi, mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Isiraeli,+ wakuti: “Bwera tidzamenyane.”+ 18 Yehoasi mfumu ya Isiraeli atamva anamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti:+ “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,+ wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’+ Koma nyama yakuthengo+ ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija. 19 Ukunena kuti wagonjetsa Edomu,+ choncho mtima wako+ wayamba kudzikuza ndi kudzitamandira.+ Khala m’nyumba mwako momwemo.+ N’chifukwa chiyani ukufuna kumenya nkhondo pamene uli wofooka?+ Iweyo ndi Ayuda amene uli nawowo mugonja.”+

20 Koma Amaziya sanamvere, popeza Mulungu woona+ ndi amene anachititsa zimenezi kuti awapereke m’manja mwa adani, chifukwa iwo anafunafuna milungu ya Edomu.+ 21 Chotero Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anabwera+ ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anamenyana+ ku Beti-semesi+ m’dziko la Yuda. 22 Pa nkhondoyo, Ayuda anagonja pamaso pa Aisiraeli+ moti aliyense anathawira kuhema wake.+ 23 Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira+ Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yehoasi, mwana wa Yehoahazi ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya n’kupita naye ku Yerusalemu,+ ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efuraimu+ mpaka kukafika pa Chipata cha Pakona.+ Anagumula mpata waukulu mikono 400. 24 Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense, ndi ziwiya zonse zimene anazipeza m’nyumba ya Mulungu woona, ndipo anatenganso Obedi-edomu+ ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anagwiranso anthu ena n’kubwerera ku Samariya.+

25 Amaziya+ mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, anakhalabe ndi moyo zaka 15 pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli.+ 26 Nkhani zina zokhudza Amaziya, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.+ 27 Amaziya atasiya kutsatira Yehova, anthu anam’konzera chiwembu+ ku Yerusalemu. Patapita nthawi iye anathawira ku Lakisi.+ Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko n’kukamuphera komweko.+ 28 Atatero anamunyamula pamahatchi+ n’kukamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake mumzinda wa Yuda.+

26 Kenako anthu onse+ a ku Yuda anatenga Uziya+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16, n’kumulonga+ ufumu m’malo mwa bambo ake Amaziya.+ 2 Mfumu itagona ndi makolo ake,+ Uziya anamanganso mzinda wa Eloti+ n’kuubwezeretsa ku Yuda. 3 Uziya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 16, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu, ndipo dzina lawo linali Yekoliya.+ 4 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Amaziya bambo ake anachita.+ 5 Uziya anali kufunafuna+ Mulungu m’masiku a Zekariya yemwe anali kumulangiza kuti aziopa Mulungu woona.+ M’masiku amene iye anafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.+

6 Iye anapita kukamenyana ndi Afilisiti+ ndipo anagumula mpanda wa ku Gati,+ wa ku Yabine+ ndi wa ku Asidodi.+ Kenako anamanga mizinda m’chigawo cha Asidodi+ ndiponso pakati pa Afilisiti. 7 Mulungu woona anapitiriza kumuthandiza+ kumenyana ndi Afilisiti, Aluya+ amene anali kukhala ku Gurubaala, ndiponso Ameyuni.+ 8 Ndiyeno Aamoni+ anayamba kupereka msonkho+ kwa Uziya. Pomalizira pake, kutchuka kwake+ kunafika mpaka ku Iguputo chifukwa anasonyeza mphamvu zochuluka zedi. 9 Kuwonjezera apo Uziya anamanga nsanja+ ku Yerusalemu pafupi ndi Chipata cha Pakona,+ Chipata cha Kuchigwa,+ ndiponso pafupi ndi Mchirikizo wa Khoma, ndipo nsanjazo anazilimbitsa. 10 Iye anamanganso nsanja+ m’chipululu ndipo anakumba zitsime zambiri (popeza anakhala ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela+ ndi kudera lokwererapo. Kumapiri ndi ku Karimeli kunali alimi ndi anthu osamalira minda ya mpesa popeza iye ankakonda ulimi.

11 Komanso Uziya anali ndi asilikali amene ankapita kunkhondo m’magulumagulu.+ Yeyeli mlembi+ ndi Maaseya anawerenga ndi kulemba mayina+ asilikali a m’magulu amenewa. Amuna awiri amenewa anali kuyang’aniridwa+ ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu.+ 12 Atsogoleri onse a nyumba za makolo awo,+ amuna amphamvu+ ndi olimba mtima,+ analipo 2,600. 13 Atsogoleri amenewa ankayang’anira gulu lankhondo la asilikali 307,500, omenya nkhondo mwamphamvu pothandiza mfumu kulimbana ndi adani.+ 14 Uziya anapitiriza kukonzera gulu lankhondo lonselo zishango,+ mikondo ing’onoing’ono,+ zisoti,+ zovala za mamba achitsulo,+ mauta,+ ndi miyala yoponya ndi gulaye.*+ 15 Kuwonjezera apo, ku Yerusalemu anapanga makina ankhondo opangidwa ndi anthu aluso, oti aziwaika pansanja+ ndi pamakona a mpanda, kuti aziponyera mivi ndi miyala ikuluikulu. Chotero anatchuka+ mpaka kutali kwambiri, popeza anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu.

16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+ 17 Nthawi yomweyo wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova okwanira 80, amuna amphamvu, anam’tsatira. 18 Kenako iwo anatsutsa mfumu Uziya+ n’kuiuza kuti: “Mfumu Uziya, si ntchito yanu+ kufukiza kwa Yehova koma ntchito yofukizayi ndi ya ansembe, ana a Aroni,+ amene anayeretsedwa. Tulukani m’nyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika, ndipo sizikubweretserani ulemerero uliwonse+ pamaso pa Yehova Mulungu.”

19 Koma Uziya anakwiya kwambiri+ atanyamula chiwaya chofukizira+ m’manja mwake. Atawakwiyira choncho ansembewo, khate+ linabuka+ pamphumi pake ali pamaso pa ansembewo m’nyumba ya Yehova pambali pa guwa lansembe zofukiza. 20 Wansembe wamkulu Azariya ndi ansembe ena onse atamuyang’ana, anangoona kuti wachita khate pamphumi.+ Choncho anayamba kumutulutsa msangamsanga, ndipo mwiniwakeyonso anatuluka mofulumira chifukwa Yehova anali atamulanga.+

21 Mfumu Uziya+ inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira. Iyo inali kungokhala m’nyumba ina chifukwa cha khatelo+ osagwiranso ntchito, popeza inali itachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Pa nthawiyi, Yotamu mwana wake ndiye anali kuyang’anira nyumba ya mfumu ndi kuweruza anthu a m’dzikolo.

22 Nkhani zina zokhudza Uziya,+ zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 23 Pomalizira pake, Uziya anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake, koma anamuika kunja kwa manda a mafumu+ chifukwa anati: “Ndi wakhate.” Kenako Yotamu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

27 Yotamu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa+ mwana wa Zadoki. 2 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Uziya bambo ake anachita,+ kungoti sanakalowe m’kachisi wa Yehova.+ Koma anthu anali kuchitabe zoipa.+ 3 Iye anamanga chipata chakumtunda+ cha nyumba ya Yehova ndipo pakhoma la Ofeli+ anamangapo zinthu zambiri. 4 M’dera lamapiri la Yuda+ anamangamo mizinda+ ndipo m’dera lankhalango+ anamangamo malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndiponso nsanja.+ 5 Yotamu anamenyana ndi mfumu ya ana a Amoni+ ndipo pomalizira pake anawaposa mphamvu. Choncho chaka chimenecho ana a Amoni anam’patsa matalente a siliva* 100 ndi tirigu+ wokwana miyezo 10,000 ya kori,*+ komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori.+ Izi n’zimene ana a Amoni anamulipira. Anamulipiranso zomwezi m’chaka chachiwiri ndi chachitatu.+ 6 Chotero Yotamu anapitiriza kulimbitsa ufumu wake, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.+

7 Nkhani zina zokhudza Yotamu,+ nkhondo zake ndi njira zake zonse, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. 8 Iye anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+ 9 Pomalizira pake, Yotamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Ahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

28 Ahazi+ anali ndi zaka 20 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16.+ Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.+ 2 Koma anayenda m’njira za mafumu a Isiraeli,+ ndipo anafika mpaka popangira Abaala+ zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.+ 3 Ahazi anafukiza nsembe yautsi+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Iye anawotcha ana ake+ pamoto mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+ 4 Nthawi ndi nthawi ankapereka nsembe+ ndi kufukiza nsembe yautsi pamalo okwezeka,+ pamapiri,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+

5 Choncho Yehova Mulungu wake anam’pereka m’manja+ mwa mfumu ya Siriya+ moti Asiriya anam’gonjetsa n’kugwira anthu ake ambiri kupita nawo ku Damasiko.+ Anam’perekanso m’manja mwa mfumu ya Isiraeli+ ndipo inam’gonjetsa n’kupha anthu ake ambirimbiri. 6 Chotero Peka+ mwana wa Remaliya+ anakapha anthu 120,000 ku Yuda tsiku limodzi. Onse amene anaphedwawo anali amuna olimba mtima. Iwo anaphedwa chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo. 7 Kuwonjezera apo, Zikiri mwamuna wamphamvu wa fuko la Efuraimu,+ anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu mtsogoleri wa nyumba ya mfumu ndiponso Elikana yemwe anali wachiwiri kwa mfumu. 8 Komanso ana a Isiraeli anagwira abale awo okwana 200,000 n’kuwatenga. Pa anthu ogwidwawo panali amayi, ana aamuna ndi ana aakazi. Anafunkhanso zinthu zawo zambiri n’kupita nazo ku Samariya.+

9 Kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi. Iye anapita kukakumana ndi asilikali omwe anali kubwerera ku Samariya n’kuwauza kuti: “Tamverani! Yehova Mulungu wa makolo anu wapereka Ayuda m’manja mwanu chifukwa chakuti anawakwiyira kwambiri.+ N’chifukwa chake inuyo mwapha anthu pakati pawo mwaukali kwambiri,+ ndipo ukaliwo wafika mpaka kumwamba.+ 10 Tsopano mukufuna kusandutsa ana a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti akhale antchito anu aamuna+ ndi aakazi. Kodi inuyo mulibe milandu kwa Yehova Mulungu wanu? 11 Tsopano tamverani! Bwezani anthu amene mwawagwira kuchokera kwa abale anuwa,+ chifukwa mkwiyo wa Yehova wakuyakirani.”+

12 Kenako amuna ena omwe anali atsogoleri+ a ana a fuko la Efuraimu,+ anaukira asilikali amene anabwera kuchokera ku nkhondowo. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu ndi Amasa mwana wa Hadilai. 13 Iwo anawauza kuti: “Musabweretse kuno anthu amene mwawagwirawo chifukwa tikhala ndi mlandu kwa Yehova. Mukufuna kuwonjezera machimo athu ndiponso mlandu wathu pakuti tili kale ndi mlandu waukulu,+ ndipo mkwiyo waukulu+ wa Mulungu wayakira Isiraeli.” 14 Choncho amuna onyamula zidawo+ anasiya anthuwo+ ndi zofunkha pamaso pa akalonga+ ndi pa mpingo wonse. 15 Kenako amuna amene anachita kusankhidwa powatchula mayina+ ananyamuka n’kutenga anthu ogwidwawo. Anthu onse amene sanavale* zovala anawaveka zovala+ zimene anafunkha ndipo anawavekanso nsapato. Anawapatsa chakudya+ ndi zakumwa,+ ndipo anawadzoza mafuta. Kuwonjezera apo, aliyense amene anali kuyenda movutikira anamukweza+ pabulu. Atatero anatenga anthuwo n’kupita nawo ku Yeriko,+ kumzinda wa mitengo ya kanjedza,+ kufupi ndi abale awo. Pambuyo pake iwo anabwerera ku Samariya.+

16 Pa nthawi imeneyo, Mfumu Ahazi+ inatumiza uthenga kwa mafumu a Asuri+ kuti adzam’thandize. 17 Aedomu+ anabweranso n’kudzapha Ayuda, ndipo anagwira anthu ena n’kuwatenga. 18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu+ n’kulanda mizinda ya Beti-semesi,+ Aijaloni,+ Gederoti,+ Soko+ ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira, komanso Gimizo ndi midzi yake yozungulira, n’kuyamba kukhala kumeneko. 19 Zinatero chifukwa chakuti Yehova anatsitsa+ Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera kuti makhalidwe oipa achuluke mu Yuda.+ Iye anachita zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.

20 M’kupita kwa nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kudzamenyana naye. Iye anam’sautsa+ ndipo sanam’limbikitse. 21 Ahazi anatenga zinthu za m’nyumba ya Yehova,+ za m’nyumba ya mfumu+ ndi za m’nyumba za akalonga,+ n’kuzipereka kwa mfumu ya Asuri+ monga mphatso, koma zimenezi sizinam’thandize. 22 Pa nthawi imene Mfumu Ahazi inali kusautsidwa, inawonjezera kuchita zosakhulupirika kwa Yehova.+ 23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu+ ya ku Damasiko+ imene inali kumuukira, ndipo anati: “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza,+ ndipereka nsembe kwa iyo kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inakhala chopunthwitsa kwa iye ndi kwa Aisiraeli onse.+ 24 Kuwonjezera apo, Ahazi anasonkhanitsa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona+ n’kuziphwanyaphwanya. Komanso anatseka zitseko+ za nyumba ya Yehova. Kenako anakadzimangira maguwa ansembe m’makona onse a mu Yerusalemu.+ 25 M’mizinda yonse ya Yuda anamangamo malo okwezeka+ operekera nsembe zautsi kwa milungu ina.+ Chotero anakwiyitsa+ Yehova Mulungu wa makolo ake.

26 Nkhani zina+ zokhudza Ahazi, zoyambirira ndi zomalizira, ndiponso njira zake zonse, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli. 27 Pomalizira pake, Ahazi anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda mumzinda, ku Yerusalemu. Iye sanaikidwe m’manda a mafumu a Isiraeli.+ Kenako Hezekiya mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

29 Hezekiya+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abiya mwana wa Zekariya.+ 2 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Davide kholo lake anachita.+ 3 M’chaka choyamba cha ulamuliro wake, m’mwezi woyamba,* iye anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova n’kuyamba kuzikonza.+ 4 Kenako anasonkhanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi pabwalo+ mbali yakum’mawa. 5 Ndiyeno anawauza kuti: “Tamverani Alevi inu. Dziyeretseni+ ndipo muyeretsenso nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Mutulutse chinthu chodetsedwa m’malo oyera.+ 6 Pakuti makolo athu achita zosakhulupirika+ ndipo achita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu.+ Iwo anamusiya+ n’kufulatira chihema chopatulika cha Yehova+ n’kulozetsako nkhongo. 7 Anatseka zitseko+ za khonde, anazimitsa nyale,+ ndiponso anasiya kupsereza zofukiza+ ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Isiraeli m’malo oyera.+ 8 Chotero mkwiyo wa Yehova+ unayakira Yuda ndi Yerusalemu, moti anawachititsa kuti akhale chinthu chonthunthumiritsa,+ chinthu chodabwitsa,+ ndiponso chinthu chochititsa anthu kuimba mluzu,+ monga momwe mukuonera ndi maso anu. 9 Pa chifukwa chimenechi, makolo athu anaphedwa ndi lupanga+ ndipo ana athu aamuna ndi aakazi ndiponso akazi athu anapita ku ukapolo.+ 10 Tsopano ineyo ndikufunitsitsa mumtima mwanga kuchita pangano+ ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli, kuti mkwiyo wake umene watiyakira utichokere. 11 Ndiyeno inu ana anga musapumule,+ chifukwa inu ndi amene Yehova wakusankhani kuti muziima pamaso pake ndi kum’tumikira+ ndiponso kuti mukhalebe atumiki ake+ ndi ofukiza nsembe yautsi.”+

12 Pamenepo Alevi+ anaimirira. Alevi ake anali Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya ochokera mwa ana a Kohati.+ Kuchokera mwa ana a Merari,+ panali Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli. Kuchokera mwa Agerisoni+ panali Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa. 13 Kuchokera mwa ana a Elizafana+ panali Simuri ndi Yeweli. Kuchokera mwa ana a Asafu+ panali Zekariya ndi Mataniya. 14 Kuchokera mwa ana a Hemani+ panali Yehiela ndi Simeyi. Kuchokera mwa ana a Yedutuni+ panali Semaya ndi Uziyeli. 15 Iwo anasonkhanitsa abale awo pamodzi n’kudziyeretsa.+ Ndiyeno anabwera kudzayeretsa+ nyumba ya Yehova mogwirizana ndi lamulo la mfumu potsatira mawu+ a Yehova. 16 Tsopano ansembe analowa m’nyumba ya Yehova kukayeretsamo, ndipo anatulutsa zonyansa zonse zimene anazipeza m’kachisi wa Yehova n’kupita nazo pabwalo+ la nyumba ya Yehova. Kenako Alevi anazitenga n’kupita nazo kunja kuchigwa cha Kidironi.+ 17 Chotero anayamba kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo pa tsiku la 8 la mweziwo anafika pakhonde+ la nyumba ya Yehova. Choncho anayeretsa nyumba ya Yehova m’masiku 8. Pa tsiku la 16 la mwezi woyamba+ anamaliza ntchitoyo.

18 Atatero analowa kumene kunali mfumu Hezekiya n’kukaiuza kuti: “Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, guwa lansembe+ zopsereza ndi ziwiya zake zonse,+ ndiponso tebulo+ loikapo mkate wosanjikiza ndi ziwiya zake zonse.+ 19 Ziwiya zonse+ zimene Mfumu Ahazi+ anasiya kuzigwiritsira ntchito mu ulamuliro wake chifukwa cha kusakhulupirika kwake,+ tazikonza ndi kuziyeretsa+ ndipo zili pafupi ndi guwa lansembe la Yehova.”

20 Tsopano mfumu Hezekiya+ inadzuka m’mawa kwambiri+ n’kusonkhanitsa akalonga+ a mzindawo, n’kupita kunyumba ya Yehova. 21 Iwo anabweretsa ng’ombe zamphongo 7,+ nkhosa zamphongo 7, ana a nkhosa amphongo 7 ndi mbuzi zamphongo 7 kuti azipereke monga nsembe yamachimo+ ya ufumuwo, ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Chotero Hezekiya anauza ana a Aroni, omwe anali ansembe,+ kuti apereke nsembeyo paguwa lansembe la Yehova. 22 Iwo anapha+ ng’ombezo ndipo ansembe anatenga magazi+ ake n’kuwaza+ paguwa lansembe. Kenako anapha nkhosa zamphongo+ zija n’kuwaza magazi ake paguwa lansembe. Atatero anapha ana a nkhosa amphongo aja n’kuwaza magazi+ ake paguwa lansembe. 23 Kenako anatenga mbuzi zamphongo+ za nsembe yamachimo zija n’kuzibweretsa pafupi ndi mfumu ndi mpingo wonse, ndipo iwo anasanjika manja awo pambuzizo.+ 24 Tsopano ansembe anazipha n’kuzipereka nsembe yamachimo pamodzi ndi magazi ake paguwa lansembe kuti aphimbe machimo a Aisiraeli onse,+ popeza mfumu inati nsembe yopsereza ndi yamachimoyo+ ikhale ya Aisiraeli onse.+

25 Pa nthawi imeneyi, Hezekiya anaika Alevi+ panyumba ya Yehova atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze.+ Iwo anali kutsatira ndondomeko yoimbira imene anaikhazikitsa Davide,+ Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndi mneneri Natani,+ popeza ndondomekoyo inachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.+ 26 Choncho Aleviwo anaimirirabe atanyamula zipangizo zoimbira+ za Davide. Iwo anaimirira pamodzi ndi ansembe omwe ananyamula malipenga.+

27 Kenako Hezekiya anawauza kuti apereke nsembe yopsereza paguwa lansembe. Atayamba kupereka nsembe yopserezayo, nyimbo+ ya Yehova inayamba kuimbidwa limodzi ndi malipenga amene ankatsatira zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Isiraeli. 28 Mpingo wonse unagwada+ n’kuwerama pamene nyimboyo inali kuimbidwa mokuwa+ ndiponso pamene malipenga anali kulizidwa mokweza. Mpingowo unakhala chowerama choncho mpaka anamaliza kupereka nsembe yopsereza. 29 Atangomaliza kupereka nsembeyo, mfumu ndi onse amene anali nayo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 30 Tsopano mfumu Hezekiya ndi akalonga+ anauza Alevi kuti atamande Yehova ndi mawu a Davide+ ndi a wamasomphenya Asafu.+ Chotero iwo anayamba kutamanda Mulungu mosangalala+ ndipo anakhalabe chogwada atawerama mpaka mphumi zawo pansi.+

31 Pomalizira pake Hezekiya anati: “Tsopano mwayeneretsedwa kuti mukhale ansembe+ otumikira Yehova. Bweretsani nsembe zoyamikira+ ndi nsembe zina+ kunyumba ya Yehova.” Ndiyeno mpingowo unayamba kubweretsa nsembe zoyamikira ndi nsembe zina, ndipo aliyense wa mtima wofunitsitsa anali kubweretsa nsembe zopsereza.+ 32 Nsembe zopsereza zimene mpingowo unabweretsa zinakwana ng’ombe 70, nkhosa zamphongo 100, ndi ana a nkhosa amphongo 200. Zonsezi anazipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza.+ 33 Anabweretsanso zopereka zopatulika zokwana ng’ombe 600 ndi nkhosa 3,000. 34 Koma ansembe+ anali ochepa kwambiri ndipo sanathe kusenda nyama zonse za nsembe zopsereza.+ Choncho abale awo+ Alevi anawathandiza mpaka ntchitoyo inatha+ ndiponso kufikira pamene ansembewo anadziyeretsa,+ popeza Alevi ankafunitsitsa kudziyeretsa kuposa ansembe.+ 35 Komanso, nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta+ a nsembe zachiyanjano+ zinali zambiri. Nazonso nsembe zachakumwa+ zimene zinaperekedwa limodzi ndi nsembe zopserezazo zinali zambiri. Chotero utumiki wa panyumba ya Yehova unakonzedwa.+ 36 Choncho Hezekiya ndi anthu onse anasangalala chifukwa Mulungu woona anathandiza anthuwo,+ pakuti zinthuzo zinachitika mosayembekezereka.+

30 Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembanso makalata ku Efuraimu+ ndi ku Manase,+ kuti abwere kunyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu kudzachita pasika+ kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. 2 Koma mfumuyo, akalonga ake+ ndi mpingo wonse+ ku Yerusalemu anagwirizana zoti achite pasikayo m’mwezi wachiwiri.+ 3 Iwo sanathe kuchita pasikayo m’mwezi woyamba+ popeza ansembe amene anadziyeretsa sanali okwanira+ komanso anthuwo sanasonkhane ku Yerusalemu. 4 Nkhaniyi inakomera mfumu ndi mpingo wonsewo.+ 5 Choncho anagwirizana kuti alengeze+ zimenezi mu Isiraeli yense kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo auze anthuwo kuti abwere ku Yerusalemu adzachite pasika kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa m’mbuyomo, iwo sanali kusonkhana onse pamodzi+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+

6 Ndiyeno asilikali othamanga+ amene anatenga makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akalonga ake,+ anapita mu Isiraeli ndi Yuda yense mogwirizana ndi lamulo la mfumu, lakuti: “Inu ana a Isiraeli, bwererani+ kwa Yehova Mulungu+ wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli, kuti iye abwerere kwa anthu anu otsala+ amene anapulumuka m’manja mwa mafumu a Asuri.+ 7 Musakhale ngati makolo anu+ ndi abale anu amene anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo, mwakuti anawachititsa kukhala chinthu chodabwitsa+ monga mmene mukuoneramu. 8 Tsopano musaumitse khosi lanu+ ngati mmene anachitira makolo anu. Gonjerani Yehova,+ pitani kunyumba yake yopatulika+ imene waiyeretsa+ mpaka kalekale. Tumikirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake umene wakuyakirani+ ukuchokereni. 9 Mukabwerera+ kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo+ ndi anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina. Chotero iwo adzaloledwa kubwerera kudziko lino+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo+ ndiponso wachifundo,+ ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwerera kwa iye.”+

10 Asilikali othamangawo+ anapitiriza ulendo wawo ndipo anapita kumzinda ndi mzinda m’dziko lonse la Efuraimu+ ndi Manase mpaka ku Zebuloni. Koma anthuwo ankangokhalira kuwatonza ndi kuwaseka.+ 11 Anthu+ ochokera ku Aseri, ku Manase, ndi ku Zebuloni okha ndi amene anadzichepetsa+ n’kubwera ku Yerusalemu. 12 Dzanja la Mulungu woona linakhalanso ndi anthu a ku Yuda, moti anawapatsa mtima umodzi+ kuti amvere lamulo+ la mfumu ndi la akalonga pa nkhani zokhudza kutumikira Yehova.+

13 Tsopano chikhamu cha anthu chinasonkhana ku Yerusalemu+ kuti achite chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa m’mwezi wachiwiri,+ ndipo unali mpingo waukulu kwambiri. 14 Kenako iwo ananyamuka n’kuchotsa maguwa ansembe+ amene anali mu Yerusalemu. Anachotsanso maguwa ansembe onse ofukizirapo+ n’kukawataya kuchigwa cha Kidironi.+ 15 Atatero anapha nyama ya pasika+ pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anali atachititsidwa manyazi moti anadziyeretsa+ n’kubweretsa nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova. 16 Iwo anaimirira+ m’malo mwawo mogwirizana ndi zimene analamulidwa, malinga ndi lamulo la Mose munthu wa Mulungu woona. Ansembe+ anali kuwaza paguwa lansembe magazi amene anali kulandira kwa Alevi. 17 Koma panali anthu ambiri mumpingowo amene sanadziyeretse. Choncho Alevi+ ndi amene anali kugwira ntchito yophera nyama za pasika+ anthu onse amene sanali oyera, kuti awayeretse kwa Yehova. 18 Panali anthu ambiri ochokera ku Efuraimu,+ ku Manase,+ ku Isakara ndi ku Zebuloni+ amene sanadziyeretse+ ndipo anadya pasikayo mosatsatira zimene zinalembedwa.+ Koma Hezekiya anawapempherera+ kuti: “Yehova wabwino+ asakwiyire 19 aliyense amene wakonza mtima wake+ kuti afunefune Mulungu woona Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti sanadziyeretse mogwirizana ndi zinthu zopatulika.”+ 20 Choncho Yehova anamvera Hezekiya ndipo anakhululukira anthuwo.+

21 Chotero ana a Isiraeli amene anali ku Yerusalemu anachita chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa masiku 7 mosangalala kwambiri.+ Alevi+ ndi ansembe+ anali kutamanda Yehova tsiku ndi tsiku ndi zipangizo zoimbira za mawu okwera zotamandira Yehova.+ 22 Kuwonjezera apo, Hezekiya analankhula mokoma mtima+ kwa Alevi onse amene anali kutumikira Yehova mwanzeru.+ Anthuwo anachita phwando loikidwiratu kwa masiku 7.+ Anali kupereka nsembe zachiyanjano+ ndi kulapa+ kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.

23 Ndiyeno mpingo wonsewo unagwirizana+ kuti uchitenso phwandolo masiku ena 7.+ Choncho analichitanso masiku 7 mosangalala. 24 Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka+ ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 7,000. Akalonganso+ anapereka ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000, ndipo ansembe+ ambiri anali kudziyeretsa. 25 Mpingo wonse wa Ayuda,+ ansembe, Alevi+ ndiponso mpingo wonse wa anthu amene anachokera ku Isiraeli,+ alendo+ amene anachokera m’dziko la Isiraeli+ ndi amene anali kukhala m’dziko la Yuda, anapitiriza kusangalala.+ 26 Chotero munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira m’masiku a Solomo+ mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanachitike chikondwerero ngati chimenechi ku Yerusalemu.+ 27 Pomalizira pake ansembe achilevi anaimirira n’kudalitsa+ anthuwo, ndipo mawu awo anamvedwa moti pemphero lawo linafika kumwamba, kumalo oyera okhala Mulungu.+

31 Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli+ onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda+ n’kukaphwanya zipilala zopatulika,+ kukadula mizati yopatulika+ ndi kukagwetsa malo okwezeka+ ndi maguwa ansembe+ mu Yuda yense,+ mu Benjamini, mu Efuraimu+ ndi m’Manase+ mpaka kumaliza ntchitoyo. Atatero, ana onse a Isiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.

2 Kenako Hezekiya anaika magulu+ a ansembe ndi Alevi+ mogwirizana ndi magulu awo. Gulu lililonse analiika mogwirizana ndi utumiki wawo monga ansembe+ ndi Alevi+ ogwira ntchito yokhudza nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ Anawaika m’maguluwa kuti azitumikira,+ kuyamika+ ndi kutamanda+ Mulungu m’zipata za kachisi wa Yehova. 3 Kuchokera pa katundu wake,+ mfumuyo inapereka nsembe zopsereza za m’mawa+ ndi za madzulo, komanso nsembe zopsereza za masabata,+ za masiku okhala mwezi+ ndi za panyengo zochita chikondwerero,+ monga gawo limene inayenera kupereka la nsembe zopsereza,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Yehova.+

4 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu okhala mu Yerusalemu kuti apereke gawo loyenera kupita kwa ansembe+ ndi Alevi,+ n’cholinga choti iwo azitsatira+ mosamala chilamulo cha Yehova.+ 5 Ana a Isiraeli+ atangomva mawuwo, anawonjezera zipatso zoyambirira zimene ankapereka za mbewu,+ vinyo watsopano,+ mafuta,+ uchi,+ ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anabweretsa chakhumi cha zonsezi chochuluka zedi.+ 6 Ana a Isiraeli ndi Yuda amene anali kukhala m’mizinda ya Yuda+ anabweretsa chakhumi cha ng’ombe, nkhosa, ndi chakhumi cha zinthu zopatulika+ zimene anaziyeretsera Yehova Mulungu wawo. Anabweretsa zinthu zimenezi zambiri mpaka kukwana milumilu. 7 M’mwezi wachitatu+ anayamba kuunjika milu ya mphatsozo, ndipo m’mwezi wa 7+ anamaliza. 8 Hezekiya ndi akalonga+ atabwera n’kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa+ anthu ake Aisiraeli.+

9 Patapita nthawi Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyo.+ 10 Ndiyeno Azariya,+ wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki,+ anamuyankha kuti: “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka+ m’nyumba ya Yehova, pakhala kudya ndi kukhuta+ ndipo pali zotsala zambiri,+ chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake+ ndipo zonse mukuzionazi n’zimene zatsala.”

11 Pamenepo Hezekiya anawauza kuti akonze zipinda zodyera+ m’nyumba ya Yehova, ndipo iwo anakonzadi. 12 Anthuwo anapitiriza kubweretsa zopereka,+ chakhumi,+ ndi zinthu zopatulika. Iwo ankabweretsa zimenezi mokhulupirika.+ Konaniya Mlevi ndiye anali kuyang’anira monga mtsogoleri, ndipo Simeyi m’bale wake anali wachiwiri wake. 13 Yehiela, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali atumiki othandiza Konaniya ndi Simeyi m’bale wake mwa lamulo la mfumu Hezekiya. Azariya+ ndiye anali mtsogoleri wa nyumba ya Mulungu woona. 14 Kore mwana wa Imuna Mlevi anali mlonda wa pachipata+ chakum’mawa+ amene anali kuyang’anira zopereka zaufulu+ zopita kwa Mulungu woona ndi kugawa zopereka za Yehova+ ndi zinthu zopatulika koposa.+ 15 Iye anali kuyang’anira Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m’mizinda ya ansembe+ amene anali pa maudindo awo chifukwa cha kukhulupirika kwawo.+ Amenewa ankagwira ntchito yogawa zinthu kwa abale awo amene anali m’magulu.+ Ankawagawira zinthuzo mofanana, kaya akhale wamkulu kapena wamng’ono.+ 16 Ankagawira anthu amenewa kuwonjezera pa amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ komanso amuna oyambira zaka zitatu kupita m’tsogolo.+ Onsewa ankabwera kunyumba ya Yehova tsiku ndi tsiku kudzachita utumiki wawo, umene anayenera kuchita mogwirizana ndi magulu awo.

17 Panali mndandanda wa mayina a ansembe wotsatira makolo awo+ ndi mndandanda wa mayina a Alevi+ kuyambira azaka 20+ kupita m’tsogolo, malinga ndi ntchito zawo m’magulu awo.+ 18 Mndandandawo unali wa ana awo onse, akazi awo, ndiponso ana awo aamuna ndi aakazi mumpingo wonsewo, pakuti pa ntchito yawo imene ankagwira chifukwa cha kukhulupirika kwawo,+ anadziyeretsa+ kuti achite utumiki wawo wa zinthu zopatulika. 19 Panalinso mndandanda wa mayina a ana a Aroni,+ ansembe, amene anali kukhala m’malo+ odyetserako ziweto kunja kwa mizinda yawo. M’mizinda yonseyo munali amuna amene anasankhidwa pochita kuwatchula mayina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa mwamuna aliyense pakati pa ansembe ndiponso kwa Alevi onse amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.

20 Hezekiya anachita zimenezi mu Yuda yense, ndipo anapitiriza kuchita zabwino,+ zoyenera+ ndi zokhulupirika+ pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21 Anagwira ndi mtima wake wonse+ ntchito iliyonse imene anaiyamba mu utumiki+ wa panyumba ya Mulungu woona ndi m’chilamulo,+ pofunafuna+ Mulungu wake, ndipo zinthu zinamuyendera bwino.+

32 Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa ntchito zokhulupirika+ za Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera n’kudzazungulira Yuda ndipo anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Iye anali kuganiza zogonjetsa mizindayo kuti ikhale yake.

2 Hezekiya ataona kuti Senakeribu wabwera n’cholinga chochita nkhondo+ ndi mzinda wa Yerusalemu, 3 anagwirizana ndi akalonga ake+ ndi amuna ake amphamvu kuti atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo,+ choncho iwo anamuthandiza. 4 Chotero anthu ambiri anasonkhana ndipo anapita kukatseka akasupe onse ndi mtsinje+ umene unkasefukira kudutsa pakati pa dzikolo, popeza anati: “Sitikufuna kuti mafumu a Asuri akabwera adzapeze madzi ochuluka.”

5 Kuwonjezera apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka.+ Anamanga nsanja+ pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina.+ Anakonzanso Chimulu cha Dothi*+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zida+ zambiri ndi zishango.+ 6 Kenako anaika akuluakulu a asilikali+ kuti aziyang’anira anthuwo, ndipo anawauza kuti akumane naye pabwalo+ la mzindawo limene linali pachipata. Kumeneko iye anawalankhula mowalimbitsa mtima+ kuti: 7 “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.+ Musaope+ kapena kuchita mantha+ ndi mfumu ya Asuri+ ndi khamu lalikulu limene ili nalo,+ chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo. 8 Iyo ikudalira mphamvu za anthu,*+ koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu+ kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.”+ Pamenepo anthuwo anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.+

9 Pambuyo pa zimenezi, Senakeribu+ mfumu ya Asuri ali ku Lakisi+ pamodzi ndi asilikali ake onse,+ anatumiza atumiki ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi kwa anthu onse okhala ku Yudeya ku Yerusalemu. Anawatuma kukanena kuti:

10 “Senakeribu mfumu ya Asuri yanena kuti,+ ‘Kodi mukudalira chiyani poti mukungokhala mosatekeseka, Yerusalemu atazunguliridwa?+ 11 Hezekiyatu+ akungokunyengererani+ kuti mufe ndi njala ndi ludzu pokuuzani kuti: “Yehova Mulungu wathu atipulumutsa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 12 Kodi si Hezekiya yemweyo amene anachotsa malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe+ kenako n’kuuza anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti: “Muziwerama+ pamaso pa guwa lansembe limodzi lokha+ ndipo nsembe yautsi muzifukiza pamenepo”?+ 13 Kodi simukudziwa zimene ineyo ndi makolo anga tinachita kwa anthu onse a mayiko ena?+ Kodi milungu+ ya mitundu ya mayiko ena inatha kupulumutsa mayiko awo m’manja mwanga? 14 Ndi mulungu uti pa milungu ya mitundu imeneyi, yomwe makolo anga anaiwononga, yemwe anatha kupulumutsa anthu ake m’manja mwanga, kuti Mulungu wanu athe kukupulumutsani m’manja mwanga?+ 15 Tsopano musalole kuti Hezekiya akupusitseni+ kapena kukunyengererani+ chonchi ndipo musamukhulupirire, chifukwa palibe ufumu uliwonse kapena mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu amene anatha kupulumutsa anthu akewo m’manja mwanga ndiponso m’manja mwa makolo anga. Ndiye mukuganiza kuti Mulungu wanu angakupulumutseni m’manja mwanga?’”+

16 Atumiki a Senakeribuwo analankhula zinthu zinanso zonyoza Yehova Mulungu woona+ ndi Hezekiya mtumiki wake. 17 lye analembanso makalata+ onyoza Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ komanso omutonza kuti: “Mofanana ndi milungu+ ya mitundu ya mayiko ena imene sinapulumutse anthu ake m’manja mwanga,+ Mulungu wa Hezekiya sapulumutsa anthu ake m’manja mwanga.” 18 Iwo+ anapitiriza kulankhula mokuwa+ m’chilankhulo cha Ayuda,+ kwa anthu a ku Yerusalemu amene anali pamwamba pa mpanda, kuti awachititse mantha+ ndi kuwasokoneza n’cholinga choti alande mzindawo. 19 Anapitiriza kulankhula monyoza+ Mulungu wa Yerusalemu+ mofanana ndi mmene ankanyozera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, yopangidwa ndi manja a anthu.+ 20 Koma mfumu Hezekiya+ ndi mneneri+ Yesaya+ mwana wa Amozi,+ anali kupempherera nkhani imeneyi+ ndi kufuulira Mulungu kumwamba kuti awapulumutse.+

21 Tsopano Yehova anatumiza mngelo+ yemwe anapha mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima,+ komanso mtsogoleri ndi mkulu wa asilikali aliyense mumsasa wa mfumu ya Asuri,+ moti mfumuyo inabwerera kwawo mwamanyazi. Kenako inalowa m’kachisi wa mulungu wake ndipo ili mmenemo, ena mwa ana ake anaipha ndi lupanga.+ 22 Chotero, Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu okhala ku Yerusalemu m’manja mwa Senakeribu mfumu ya Asuri+ komanso m’manja mwa ena onse, ndipo anawapatsa mpumulo kwa adani awo onse owazungulira.+ 23 Pambuyo pa zimenezi, panali anthu ambiri amene ankabweretsa mphatso+ kwa Yehova ku Yerusalemu ndi zinthu zabwinozabwino kwa Hezekiya mfumu ya Yuda,+ moti iye anakwezeka+ m’maso mwa mitundu yonse.

24 M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa,+ ndipo anapemphera+ kwa Yehova. Choncho iye analankhula ndi Hezekiya+ n’kumupatsa chizindikiro cholosera zam’tsogolo.+ 25 Koma Hezekiya sanabwezere zabwino zimene anachitiridwa,+ pakuti mtima wake unayamba kudzikuza+ ndipo mkwiyo wa Mulungu+ unayakira iyeyo, Yuda, ndi Yerusalemu. 26 Komabe, Hezekiya anadzichepetsa+ pambuyo pa kudzikuza kwa mtima wake. Anadzichepetsa limodzi ndi anthu a ku Yerusalemu, ndipo mkwiyo wa Yehova sunawagwere m’masiku a Hezekiya.+

27 Hezekiya anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka zedi.+ Anadzimangira nyumba zosungiramo siliva, golide,+ miyala yamtengo wapatali,+ mafuta a basamu,+ zishango,+ ndi zinthu zonse zabwinozabwino.+ 28 Anamanganso mosungira+ mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta, ndipo anamanganso makola+ a zinyama zonse zosiyanasiyana ndi a magulu a ziweto. 29 Anakhala ndi mizinda ndiponso nkhosa+ ndi ng’ombe+ zochuluka, chifukwa Mulungu anam’patsa katundu wambiri.+ 30 Hezekiya ndiye anatseka+ kasupe wapamtunda wa madzi+ a ku Gihoni+ ndipo anawapatutsa n’kuwalunjikitsa kumunsi kumadzulo, ku Mzinda wa Davide.+ Ntchito iliyonse imene Hezekiya anali kuchita inali kumuyendera bwino.+ 31 Ndiyeno zinachitika kuti pamene akalonga a ku Babulo+ anatumiza nthumwi zawo kwa iye,+ kuti zikam’funse za chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ chimene chinachitika m’dzikolo, Mulungu woona anamusiya+ kuti amuyese+ ndi kuona zonse zimene zinali mumtima mwake.+

32 Nkhani zina+ zokhudza Hezekiya ndi zochita zake zosonyeza kukoma mtima kosatha,+ zinalembedwa m’masomphenya a mneneri Yesaya mwana wa Amozi,+ m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli. 33 Pomalizira pake, Hezekiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda pachitunda chopita kumanda a ana a Davide.+ Pamaliro ake, Ayuda onse ndi anthu okhala ku Yerusalemu anamusonyeza ulemu waukulu.+ Kenako Manase+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

33 Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+

2 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa+ za mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+ 3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka+ amene Hezekiya bambo ake anagwetsa.+ Anamanga maguwa ansembe+ a Abaala+ n’kumanga mizati yopatulika,+ ndipo anayamba kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+ 4 Anamanga maguwa ansembe+ m’nyumba ya Yehova, imene ponena za iyo Yehova anati: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+ 5 Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo+ m’mabwalo+ awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,+ ankachita zanyanga,+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.+

7 Komanso iye anaika m’nyumba ya Mulungu woona+ chifaniziro+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo, Mulungu anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha+ pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa+ mpaka kalekale.+ 8 Sindidzachotsanso phazi la Isiraeli panthaka imene ndinapatsa+ makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo+ chonse, malangizo+ onse, ndi zigamulo+ zonse zimene ndinawapatsa kudzera m’manja mwa Mose.”+ 9 Koma Manase+ anapitiriza kunyengerera Yuda+ ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.+

10 Yehova anapitiriza kulankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanamvere.+ 11 Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo. 12 Iye atasautsika mumtima mwake chifukwa cha zimenezi,+ anakhazikitsa pansi mtima wa Yehova Mulungu wake+ ndipo anadzichepetsa+ kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+

14 Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja+ kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira m’chigwa kukafika ku Chipata cha Nsomba.+ Mpandawo unazungulira n’kukafika ku Ofeli+ ndipo unali wautali kwambiri kuchokera pansi kufika pamwamba. Kuwonjezera apo, iye anaika akuluakulu a asilikali m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 15 Anachotsa milungu yachilendo,+ fano+ limene linali m’nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse ansembe+ amene anamanga m’phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu. Kenako, zinthu zimenezi anakazitaya kunja kwa mzinda. 16 Komanso Manase anakonza guwa lansembe la Yehova+ n’kuyamba kuperekerapo nsembe zachiyanjano+ ndi zoyamikira,+ ndipo anauza Ayuda kuti azitumikira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 17 Komabe anthu anali kuperekabe nsembe m’malo okwezeka,+ kungoti anali kuzipereka kwa Yehova Mulungu wawo.

18 Nkhani zina zokhudza Manase, pemphero+ limene anapereka kwa Mulungu wake, ndi mawu a anthu amasomphenya+ amene anali kulankhula naye m’dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, zatchulidwa m’nkhani za mafumu a Isiraeli.+ 19 Nkhani zokhudza pemphero lake,+ zokhudza mmene Mulungu anamvera kupembedza kwake,+ machimo ake onse,+ ndi kusakhulupirika kwake+ zinalembedwa m’mawu a amasomphenya ake. M’mawu amenewa munalembedwanso nkhani zokhudza malo amene iye anamangako malo okwezeka+ n’kuikapo mizati yopatulika+ ndi zifaniziro zogoba+ asanadzichepetse.+ 20 Pomalizira pake Manase anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda+ panyumba yake. Kenako Amoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

21 Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ 22 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ monga anachitira Manase bambo ake.+ Amoni anali kupereka nsembe+ kwa zifaniziro zonse zogoba+ zimene bambo ake+ anapanga, ndipo anapitiriza kuzitumikira.+ 23 Iye sanadzichepetse+ pamaso pa Yehova monga anadzichepetsera Manase bambo ake,+ pakuti Amoni ndiye amene anawonjezera kupalamula.+ 24 Pomalizira pake, atumiki ake anam’chitira chiwembu+ n’kumupha m’nyumba mwake momwe.+ 25 Koma anthu a m’dzikolo anapha+ anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni.+ Kenako anthu+ a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake.

34 Yosiya+ anali ndi zaka 8+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+ 2 Iye anachita zoyenera pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda m’njira za Davide kholo lake.+ Sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.+

3 M’chaka cha 8 cha ulamuliro wa Yosiya, iye akadali mnyamata,+ anayamba kufunafuna+ Mulungu wa Davide kholo lake. M’chaka cha 12 anayamba kuyeretsa+ Yuda ndi Yerusalemu pochotsa malo okwezeka,+ mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula. 4 Kuwonjezera apo, anthu anagwetsa maguwa ansembe+ a Abaala+ pamaso pake, ndipo zofukizira+ zimene zinali pamwamba pa maguwawo iye anazigumula. Mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula, anaziphwanya n’kuziperapera.+ Phulusa lakelo analiwaza pamanda a anthu amene anali kupereka nsembe kwa zinthu zimenezi.+ 5 Mafupa+ a ansembe anawatentha pamaguwa awo ansembe.+ Choncho Yosiya anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.

6 Komanso, m’mizinda ya Manase,+ Efuraimu,+ Simiyoni, mpaka Nafitali, ndi m’malo onse owonongedwa ozungulira mizindayi, 7 Yosiya anagwetsamo maguwa ansembe+ ndi mizati yopatulika.+ Zifaniziro zogoba+ anaziphwanya n’kuziperapera,+ ndipo anagumula zofukizira zonse+ m’dziko lonse la Isiraeli. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

8 M’chaka cha 18+ cha ulamuliro wake, atayeretsa dzikolo ndi nyumba ya Mulungu, iye anatuma Safani+ mwana wa Azaliya, Maaseya mkulu wa mzinda, ndi Yowa mwana wa Yowahazi wolemba zochitika, kuti akakonze+ nyumba ya Yehova Mulungu wake. 9 Iwo anapita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe n’kukapereka ndalama zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi omwe anali alonda a pakhomo,+ anatolera ku fuko la Manase,+ la Efuraimu,+ kwa Aisiraeli onse,+ kwa Ayuda onse, ku fuko la Benjamini, ndi kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu. 10 Kenako anapereka ndalamazo m’manja mwa ogwira ntchito osankhidwa a m’nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno iwowa anapereka ndalamazo kwa anthu amene anali kugwira ntchito m’nyumba ya Yehova, omwe anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. 11 Anthu ogwira ntchitowa anapereka ndalamazo kwa amisiri ndi kwa omanga+ nyumba kuti agulire miyala yosema+ ndi matabwa opangira zida zomangira zinthu pamodzi, ndiponso kuti akhome mitanda m’nyumba zimene mafumu+ a Yuda anazilekerera kuti ziwonongeke.

12 Anthuwo anali kugwira ntchitoyo mokhulupirika.+ Atsogoleri awo oti aziwayang’anira anali Yahati ndi Obadiya, omwe anali Alevi ochokera mwa ana a Merari,+ ndiponso Zekariya ndi Mesulamu ochokera mwa ana a Akohati.+ Aleviwo, amene aliyense wa iwo anali katswiri wodziwa kuimba ndi zipangizo zoimbira,+ 13 anali kuyang’anira+ anthu onyamula katundu+ ndi anthu onse ogwira ntchito zosiyanasiyana. Panalinso Alevi+ amene anali alembi,+ akapitawo, ndi alonda a pazipata.+

14 Pamene anali kutulutsa ndalama+ zimene zinali kubwera kunyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya+ anapeza buku+ la chilamulo cha Yehova+ loperekedwa ndi dzanja la Mose.+ 15 Chotero Hilikiya anauza Safani+ mlembi kuti: “Ndapeza buku la chilamulo m’nyumba ya Yehova!” Pamenepo Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani. 16 Tsopano Safani anapititsa bukulo kwa mfumu n’kuiuza kuti: “Atumiki anu akuchita zonse zimene zaikidwa m’manja mwawo. 17 Iwo akumakhuthula ndalama zimene akuzipeza m’nyumba ya Yehova n’kuzipereka m’manja mwa amuna osankhidwa ndiponso m’manja mwa ogwira ntchito.”+ 18 Kenako Safani mlembi anauza mfumuyo kuti: “Pali buku+ limene wansembe Hilikiya wandipatsa.”+ Ndiyeno Safani anayamba kuwerenga bukulo pamaso pa mfumu.+

19 Mfumuyo itangomva mawu a chilamulowo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.+ 20 Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya,+ Ahikamu+ mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani+ mlembi,+ ndi Asaya+ mtumiki wa mfumu, kuti: 21 “Pitani mukafunsire+ kwa Yehova m’malo mwa ineyo,+ ndiponso m’malo mwa anthu amene atsala mu Isiraeli ndi mu Yuda. Mukafunse zokhudza mawu a m’buku+ limene lapezekali, chifukwa mkwiyo wa Yehova+ umene akuyenera kutitsanulira ndi waukulu, popeza makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite zonse zimene zinalembedwa m’buku ili.”+

22 Chotero Hilikiya pamodzi ndi anthu amene mfumu inatchula anapita kukanena zimenezi kwa Hulida+ mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe anali wosamalira zovala,+ mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, ndipo Hulidayo anali kukhala kumbali yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu. 23 Iye anawauza kuti:

“Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kauzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti: 24 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka+ pamalo ano ndi anthu ake,+ pokwaniritsa matemberero onse+ amene analembedwa m’buku limene anawerenga pamaso pa mfumu ya Yuda,+ 25 chifukwa chakuti andisiya+ n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse+ ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho nditsanulira mkwiyo wanga+ pamalo ano ndipo suzimitsidwa.’”+ 26 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Ponena za mawu+ amene wamvawo, 27 chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Mulungu utamva mawu ake okhudza malo ano ndi anthu ake, ndipo unadzichepetsa pamaso panga+ n’kung’amba+ zovala zako ndi kulira pamaso panga, ineyo ndamva,+ ndiwo mawu a Yehova. 28 Ine ndidzakugoneka pamodzi ndi makolo ako, ndipo ndithu udzaikidwa m’manda ako mu mtendere.+ Maso ako sadzaona tsoka+ lonse limene ndikulibweretsa pamalo ano ndi anthu ake.’”’”+

Anthuwo anabweretsa mawuwo kwa mfumuyo. 29 Ndiyeno mfumuyo inatumiza uthenga kwa akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu n’kuwasonkhanitsa pamodzi.+ 30 Itatero, mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova+ limodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ Alevi, ndi anthu onse, wamng’ono ndi wamkulu yemwe. Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku la pangano limene linapezeka panyumba ya Yehova.+ 31 Mfumuyo inaimirirabe pamalo ake+ ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo+ ake ndi maumboni*+ ake. Inanenanso kuti idzachita+ zimenezi ndi mtima wake wonse+ ndi moyo wake wonse,+ mogwirizana ndi mawu a pangano olembedwa m’bukulo.+ 32 Kuwonjezera apo, mfumuyo inachititsa onse amene anali ku Yerusalemu ndi ku Benjamini kuti avomereze panganolo. Anthu okhala ku Yerusalemuwo anachita mogwirizana ndi pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.+ 33 Atatero, Yosiya anachotsa zonyansa zonse+ m’mayiko onse a ana a Isiraeli.+ Anachititsanso anthu onse amene anali mu Isiraeli kuti ayambe kutumikira Yehova Mulungu wawo. M’masiku ake onse, iwo sanasiye kutsatira Yehova Mulungu wa makolo awo.+

35 Kenako Yosiya+ anachita pasika+ wa Yehova ku Yerusalemu, ndipo iwo anapha nyama ya pasika+ pa tsiku la 14+ la mwezi woyamba.+ 2 Choncho iye anaika ansembe pa ntchito zawo+ ndipo anawalimbikitsa+ pa utumiki wawo wa panyumba ya Yehova.+ 3 Ndiyeno anauza Alevi, alangizi+ a Isiraeli yense, omwe anali oyera kwa Yehova, kuti: “Ikani Likasa lopatulika+ m’nyumba+ imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli anamanga. Lisakhalenso katundu wolemera pamapewa anu.+ Tsopano tumikirani+ Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisiraeli. 4 Konzekerani potsatira nyumba ya makolo anu+ mogwirizana ndi magulu anu,+ malinga ndi zimene analemba+ Davide mfumu ya Isiraeli ndiponso zimene analemba+ Solomo mwana wake. 5 Muime+ m’malo oyera potsatira magulu a nyumba ya makolo anu kuti mutumikire abale anu, ana a anthuwa, ndipo gulu lililonse la anthu likhale ndi gulu lake la Alevi+ loti liziwatumikira, losankhidwa potsatira makolo awo.+ 6 Muphe nyama ya pasika+ n’kudziyeretsa+ ndipo muikonzere abale anu kuti muchite mogwirizana ndi mawu a Yehova kudzera mwa Mose.”+

7 Tsopano Yosiya anapereka kwa ana a anthuwo ziweto zokwana 30,000, zomwe zinali ana a nkhosa amphongo ndi ana a mbuzi amphongo. Anapereka zonsezo kuti zikhale nyama zophera pasika za onse amene analipo, ndiponso ng’ombe 3,000.+ Zonsezi zinachokera pa katundu wa mfumu.+ 8 Akalonga ake+ anapereka nsembe yaufulu kwa anthuwo,+ kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ng’ombe 300 kuti zikhale nyama zophera pasika. 9 Konaniya limodzi ndi Semaya ndi Netaneli abale ake komanso Hasabiya, Yeyeli ndi Yozabadi, amene anali akulu a Alevi, anapereka kwa Alevi nkhosa ndi mbuzi 5,000 ndiponso ng’ombe 500 kuti zikhale nyama zophera pasika.

10 Iwo anamaliza kukonzekera+ ndipo ansembe anaimirirabe+ m’malo awo,+ komanso Alevi anali m’magulu awo+ mogwirizana ndi lamulo la mfumu.+ 11 Atatero anapha nyama ya pasika+ ndipo ansembe+ anawaza+ paguwa lansembe magazi amene anali kupatsidwa, pamene Alevi anali kusenda nyamazo.+ 12 Kuwonjezera apo, anakonza nsembe zopsereza kuti azipereke kwa ana a anthuwo potsatira magulu+ a nyumba ya makolo awo,+ kuti ziperekedwe+ kwa Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku la Mose.+ Anachitanso chimodzimodzi ndi ng’ombe. 13 Kenako anaphika+ nsembe ya pasika+ pamoto malinga ndi mwambo wawo ndipo zinthu zopatulika anaziphika+ m’miphika, m’miphika ya pansi pozungulira ndi m’miphika yosalowa kwambiri. Atatero anapititsa nyamayo msangamsanga kwa ana onse a anthuwo.+ 14 Pambuyo pake anakonza nyama yawo ndi ya ansembe+ chifukwa ansembe, ana a Aroni, anali otanganidwa ndi kupereka nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta+ mpaka usiku. Choncho Alevi anakonza+ nyama yawo ndi ya ansembe, ana a Aroni.

15 Oimba,+ ana a Asafu,+ anali pa ntchito yawo mogwirizana ndi lamulo la Davide,+ la Asafu,+ la Hemani+ ndi la Yedutuni+ wamasomphenya+ wa mfumu. Alonda a pazipata+ anali pazipata zosiyanasiyana.+ Panalibe chifukwa choti asiyire ntchito yawo chifukwa abale awo Alevi anawakonzera+ nyama yawo. 16 Iwo anamaliza kukonza zonse zofunikira pochita pasika+ wa Yehova tsiku limenelo, ndi popereka nsembe zopsereza paguwa lansembe la Yehova, mogwirizana ndi lamulo la Mfumu Yosiya.+

17 Ana a Isiraeli amene analipo anachita pasika+ pa nthawi imeneyo. Anachitanso chikondwerero cha mkate wopanda chofufumitsa kwa masiku 7.+ 18 Panali pasanachitikepo pasika ngati ameneyu mu Isiraeli kuyambira m’masiku a mneneri Samueli.+ Mafumu ena onse+ a Isiraeli anali asanachitepo pasika ngati amene anachita Yosiya, ansembe, Alevi, Ayuda ndi Aisiraeli onse amene analipo, ndiponso anthu okhala mu Yerusalemu. 19 Pasika ameneyu anachitika m’chaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.+

20 Pambuyo pa zonsezi, Yosiya atakonza nyumba ya Mulungu, Neko+ mfumu ya Iguputo+ anabwera kudzachita nkhondo ku Karikemisi+ pafupi ndi mtsinje wa Firate, ndipo Yosiya+ anapita kukakumana naye.+ 21 Pamenepo Neko anatumiza anthu kwa iye kukamuuza kuti: “Kodi ndili nawe chiyani iwe mfumu ya Yuda? Lero sindinabwere kudzamenyana ndi iweyo. Ndabwera kudzamenyana ndi mtundu wina umene Mulungu wanena kuti ndikauwopseze. Ngati ukufuna kuti zinthu zikuyendere bwino, usachite zimenezi. Uope Mulungu amene ali nane ndipo usalole kuti iye akuwononge.”+ 22 Koma Yosiya anapitabe kukakumana naye+ ndipo anadzisintha+ kuti amenyane naye. Iye sanamvere mawu a Neko+ ochokera pakamwa pa Mulungu. Choncho anapita kukamenyana naye m’chigwa cha Megido.+

23 Kenako asilikali oponya mivi+ analasa Mfumu Yosiya. Choncho mfumuyo inauza atumiki ake kuti: “Nditsitseni pakuti ndavulala kwambiri.”+ 24 Atumiki akewo anamutsitsa m’galetalo n’kumukweza m’galeta lake lachiwiri lankhondo, n’kupita naye ku Yerusalemu.+ Choncho iye anafa+ ndipo anamuika m’manda a makolo ake.+ Ayuda onse ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu anamulira+ Yosiya. 25 Yeremiya+ anayamba kuimbira Yosiya nyimbo ya maliro.+ Oimba onse aamuna ndi aakazi+ amanenabe za Yosiya m’nyimbo zawo zoimba polira mpaka lero. Nyimbo zimenezi zinakhazikitsidwa ngati lamulo mu Isiraeli, ndipo zinalembedwa m’nyimbo zoimba polira.+

26 Nkhani zina+ zokhudza Yosiya ndi zochita zake zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha,+ zimene anachita potsatira zomwe zinalembedwa m’chilamulo+ cha Yehova, 27 ndiponso zochita zake, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.

36 Kenako anthu a m’dzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya n’kumulonga ufumu ku Yerusalemu m’malo mwa bambo ake.+ 2 Yehoahazi anali ndi zaka 23 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ 3 Koma mfumu ya Iguputo inamuchotsa pa udindo wake ku Yerusalemu,+ n’kulamula dzikolo kuti limupatse matalente 100 a siliva*+ ndi talente imodzi ya golide.* 4 Kuwonjezera apo, mfumu+ ya Iguputo inaika Eliyakimu+ m’bale wa Yehoahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehoahazi m’bale wakeyo, Neko+ anam’tenga n’kupita naye ku Iguputo.+

5 Yehoyakimu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.+ 6 Kenako Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ kudzam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.+ 7 Ziwiya zina+ za m’nyumba ya Yehova, Nebukadinezara+ anapita nazo ku Babulo n’kukaziika m’nyumba yake yachifumu.+ 8 Nkhani zina+ zokhudza Yehoyakimu ndi zonyansa+ zimene anachita, ndiponso zoipa zimene zinapezedwa zokhudza iye, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. Kenako Yehoyakini+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

9 Yehoyakini+ anali ndi zaka 18 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu+ ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10 Kumayambiriro+ kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma+ asilikali ake omwe anakamutenga n’kubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwinozabwino za m’nyumba ya Yehova.+ Kuwonjezera apo, Nebukadinezara analonga ufumu Zedekiya+ yemwe anali m’bale wa bambo ake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+

11 Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ 12 Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova Mulungu wake, ndipo sanadzichepetse+ pamaso pa mneneri+ Yeremiya+ yemwe anapita kwa iye molamulidwa ndi Yehova. 13 Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anapandukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inali itamulumbiritsa kwa Mulungu,+ ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake+ kuti asabwerere kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. 14 Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+

15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+ 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.

17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ m’nyumba yopatulika.+ Sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu.+ Mulungu anapereka zonse m’manja mwake. 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo. 19 Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona+ ndi kugwetsa mpanda+ wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino,+ mpaka zonse zinawonongedwa.+ 20 Kuwonjezera apo, Nebukadinezara anagwira anthu amene sanaphedwe ndi lupanga ndipo anawatenga kupita nawo ku Babulo.+ Anthuwo anakakhala antchito+ ake ndi a ana ake kufikira pamene ufumu wa Perisiya+ unayamba kulamulira. 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linali kusunga sabata mpaka linakwaniritsa zaka 70.+

22 M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya,+ Yehova analimbikitsa mtima+ wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova+ kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti: 23 “Koresi mfumu ya Perisiya+ wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu m’dziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira,+ Yehova Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite.’”+

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati, “mahosi” kapena “akavalo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Kapena kuti “ya tsindwi.”

Ena amati, “chipupa” kapena “chikupa.”

Onani Zakumapeto 12.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

“Makangaza,” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Mawu ake enieni, “nyanja yosungunula.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Onani mawu a m’munsi pa Le 17:7.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “pangano la mchere.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29

Mawu ake enieni, “popunthira mbewu.”

Kutanthauza Nyanja Yofiira.

Dzinali limatanthauza, “Dalitso.”

Ahaziya ameneyu ndi “Yehoahazi” pa 2Mb 21:17.

Ameneyu akutchedwa “Ahaziya” pa vesi 1, 2, 7-11.

Onani Zakumapeto 12.

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Kapena kuti, “anavala zovala zamkati zokha.”

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pa kalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.

Mawu ake enieni, “dzanja la thupi lanyama.”

Mawu ake enieni, “anadutsitsa.”

Kapena kuti “zikumbutso.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena