Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Nehemiah 1:1-13:31
  • Nehemiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nehemiya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nehemiya

Nehemiya*

1 Awa ndi mawu a Nehemiya+ mwana wa Hakaliya. M’mwezi wa Kisilevi,*+ m’chaka cha 20,+ ine ndinali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ 2 Ndiyeno Haneni+ mmodzi mwa abale anga anabwera pamodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa+ mmene zinthu zinalili kwa gulu la Ayuda+ amene anathawa+ ku ukapolo+ komanso ndinawafunsa za Yerusalemu. 3 Chotero anandiuza kuti: “Anthu otsala amene ali m’chigawo,*+ amene anathawa ku ukapolo, ali pamavuto aakulu+ ndipo akunyozedwa.+ Nawonso mpanda+ wa Yerusalemu unagwa ndipo zipata+ zake zinatenthedwa ndi moto.”

4 Ndiyeno nditangomva mawu amenewa, ndinakhala pansi n’kuyamba kulira. Kwa masiku angapo ndinali kulira, kusala kudya+ ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wakumwamba.+ 5 Pamenepo ndinati: “Inu Yehova Mulungu wakumwamba, ndinu Mulungu wamkulu ndi wochititsa mantha.+ Anthu amene amakukondani+ ndi kusunga malamulo anu+ mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha. 6 Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu+ kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu+ limene ndikupemphera pamaso panu lero. Usana ndi usiku+ ndikupempherera atumiki anu, ana a Isiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza+ machimo+ a ana a Isiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine pamodzi ndi nyumba ya bambo anga.+ 7 Mosakayikira tachita zinthu zolakwika pamaso panu+ ndipo sitinasunge malamulo,+ malangizo+ ndi zigamulo+ zimene munapatsa mtumiki wanu Mose.+

8 “Chonde, kumbukirani+ mawu amene munauza mtumiki wanu Mose kuti, ‘Mukadzachita zinthu mosakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.+ 9 Mukadzabwerera kwa ine+ ndi kusunga malamulo anga,+ ngakhale anthu omwazikana a mtundu wanu atakhala kumalekezero a kumwamba, ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko+ ndi kuwabweretsa+ kumalo amene ndasankha kuikako dzina langa.’+ 10 Iwo ndi atumiki anu+ ndi anthu anu,+ amene munawawombola ndi mphamvu zanu zazikulu+ ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11 Aa, Yehova. Chonde, tcherani khutu ku pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero+ la atumiki anu amene amasangalala ndi kuopa dzina lanu.+ Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero+ ndipo mwamunayu andimvere chisoni.”+

Pa nthawi imeneyi, ine ndinali woperekera chikho+ kwa mfumu.

2 Ndiyeno tsiku lina m’mwezi wa Nisani,*+ m’chaka cha 20+ cha mfumu Aritasasita,+ mfumuyo inali kufuna vinyo. Pamenepo ine ndinatenga vinyoyo ndi kum’pereka kwa mfumu monga mwa nthawi zonse.+ Koma ndinali ndisanakhalepo wachisoni pamaso pake.+ 2 Ndiyeno mfumu inati: “N’chifukwa chiyani nkhope yako ili yachisoni+ pamene sukudwala? Pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.”+ Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri.

3 Pamenepo ndinayankha mfumuyo kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!+ Kodi nkhope yanga ilekerenji kukhala yachisoni pamene mzinda+ umene makolo anga+ anaikidwako uli bwinja ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto?”+ 4 Poyankha, mfumuyo inandifunsa kuti: “Ndiye ukufuna chiyani?”+ Nthawi yomweyo ndinapemphera+ kwa Mulungu wakumwamba.+ 5 Kenako ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu,+ ndipo ngati ine mtumiki wanu mungandikomere mtima,+ munditumize ku Yuda, kumzinda umene makolo anga anaikidwako kuti ndikaumangenso.”+ 6 Mfumu inandiyankha kuti: “Ulendo wako udzatenga masiku angati, ndipo udzabwera liti?” Pa nthawiyi, mkazi wamkulu wa mfumu anali atakhala pambali pake. Choncho mfumu inandilola kupita nditaiuza nthawi.+

7 Ndiyeno ndinauzanso mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, lolani kuti ndipatsidwe makalata+ okasonyeza kwa abwanamkubwa+ a tsidya lina la Mtsinje,*+ kuti akandilole kudutsa ndi kukafika ku Yuda. 8 Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyang’anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira zipata za Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ ya kukachisi,+ mpanda+ wa mzindawo ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo, chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+

9 Pambuyo pake ndinafika kwa abwanamkubwa+ kutsidya lina la Mtsinje ndi kuwapatsa makalata a mfumu. Kuwonjezera apo, mfumu inandipatsa akuluakulu a gulu lankhondo ndi asilikali okwera pamahatchi* kuti ndiyende nawo. 10 Sanibalati+ wa ku Beti-horoni+ ndi Tobia,+ mtumiki wachiamoni,+ atamva zimenezi anaipidwa kwambiri+ kuti kwabwera munthu wofunira ana a Isiraeli zabwino.

11 Patapita nthawi, ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Ndiyeno ndinadzuka usiku pamodzi ndi amuna angapo amene ndinali nawo. Sindinauze munthu aliyense+ zimene Mulungu wanga anali kuika mumtima mwanga zoti ndichitire Yerusalemu,+ ndipo ndinalibe chiweto chilichonse kupatulapo chiweto chimene ndinakwerapo. 13 Usikuwo ndinatulukira pa Chipata cha Kuchigwa,+ kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu* ndi kulowera ku Chipata cha Kumilu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinali kuonetsetsa+ mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera zipata zake.+ 14 Ndinayendabe mpaka kukafika ku Chipata cha Kukasupe+ ndi ku Dziwe la Mfumu, ndipo kumeneko kunalibe njira imene chiweto chimene ndinakwerapo chikanadutsa. 15 Koma usikuwo ndinayendabe mokwezeka m’chigwamo+ ndipo ndinapitirizabe kuonetsetsa mpandawo. Kenako ndinabwerera ndi kukalowanso pa Chipata cha Kuchigwa.+

16 Atsogoleri+ a kumeneko sanadziwe kumene ndapita ndi zimene ndinali kuchita. Komanso Ayuda pamodzi ndi ansembe, anthu olemekezeka, atsogoleri ndi ena onse amene akanagwira ntchito yomanga mpanda ndinali ndisanawauze kalikonse. 17 Pamapeto pake ndinawauza kuti: “Inu mukuona vuto lalikulu limene tili nalo. Mukuona kuti Yerusalemu ali bwinja ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto. Tiyeni timange mpanda wa Yerusalemu kuti anthu asiye kutitonza.”+ 18 Ndinawauzanso mmene dzanja+ la Mulungu wanga lachitira zinthu zabwino kwa ine+ ndiponso mawu amene mfumu inandiuza.+ Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timange mpandawo.” Choncho analimbitsa manja awo kuti agwire ntchito yabwinoyi.+

19 Ndiyeno Sanibalati+ wa ku Beti-horoni, Tobia+ mtumiki+ wachiamoni+ ndi Gesemu+ Mluya+ atamva zimenezi anayamba kutinyoza+ ndi kutiyang’ana moipidwa. Iwo anati: “N’chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mukupandukira mfumu?”+ 20 Koma ine ndinawayankha kuti: “Mulungu wakumwamba+ ndi amene adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino,+ ndipo ife atumiki ake tipitiriza kumanga mpandawu. Inu mulibe gawo,+ ufulu kapena chilichonse chokukumbukirani nacho+ mu Yerusalemu.”

3 Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Chipata cha Nkhosa.+ Iwo anapatula mbali imeneyi+ ndi kuika zitseko zake. Anapatula mbali imeneyi mpaka ku Nsanja ya Meya+ ndi Nsanja ya Hananeli.+ 2 Amuna a ku Yeriko+ nawonso anamanga kuyambira pamene Eliyasibu ndi abale ake analekezera. Kenako, Zakuri mwana wamwamuna wa Imiri, anamanga kuyambira pamene amuna a ku Yeriko analekezera.

3 Ana aamuna a Haseneya anamanga Chipata cha Nsomba.+ Iwo anachipangira felemu lamatabwa+ ndi kuika zitseko zake,+ akapichi ake ndi mipiringidzo yake.+ 4 Ndiyeno Meremoti+ mwana wamwamuna wa Uliya,+ mwana wamwamuna wa Hakozi, anakonza mpandawo kuchokera pamene ana aamuna a Haseneya analekezera. Kenako, Mesulamu+ mwana wamwamuna wa Berekiya, mwana wamwamuna wa Mesezabele, anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. Kenako, Zadoki mwana wamwamuna wa Baana, anakonza mpandawo kuchokera pamene Mesulamu analekezera. 5 Ndiyeno Atekowa+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Zadoki analekezera. Koma anthu otchuka pakati pa Atekowa+ sanagonjere ambuye awo ndi kuwatumikira.

6 Ndiyeno Yoyada mwana wamwamuna wa Paseya, komanso Mesulamu mwana wamwamuna wa Besodeya, anakonza Chipata cha Mzinda Wakale.+ Iwo anachipangira felemu lamatabwa ndi kuika zitseko zake, akapichi ake ndi mipiringidzo yake.+ 7 Kenako Melatiya Mgibeoni+ ndi Yadoni Mmeronoti+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Yoyada ndi Mesulamu analekezera. Amenewa anali amuna a ku Gibeoni+ ndi Mizipa+ amene anali pansi pa ulamuliro wa bwanamkubwa+ wa kutsidya la Mtsinje.+ 8 Kenako Uziyeli mwana wamwamuna wa Harihaya, mmodzi wa osula golide,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene winayo analekezera. Ndiyeno Hananiya mmodzi wa opanga mafuta onunkhira,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Uziyeli analekezera. Iwo anayala miyala mu Yerusalemu mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 9 Kenako Refaya mwana wamwamuna wa Hura, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anakonza mpandawo kuchokera pamene Hananiya analekezera. 10 Ndiyeno Yedaya mwana wamwamuna wa Harumafi anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake+ kuchokera pamene Refaya analekezera. Kenako Hatusi mwana wamwamuna wa Hasabineya anakonza mpandawo kuchokera pamene Yedaya analekezera.

11 Malikiya mwana wamwamuna wa Harimu,+ komanso Hasubu mwana wamwamuna wa Pahati-mowabu,+ anakonza gawo lina la mpandawo, ndipo anakonzanso Nsanja ya Mauvuni.+ 12 Kenako Salumu mwana wamwamuna wa Halohesi, kalonga+ wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anakonza mpandawo pamodzi ndi ana ake aakazi kuchokera pamene winayo analekezera.

13 Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa+ anakonza Chipata cha Kuchigwa.+ Iwo anachimanga ndi kuika zitseko zake,+ akapichi ake+ ndi mipiringidzo yake.+ Iwo anakonzanso mpandawo mikono* 1,000 mpaka kukafika ku Chipata cha Milu ya Phulusa.+ 14 Malikiya mwana wamwamuna wa Rekabu, kalonga wa chigawo cha Beti-hakeremu,+ anakonza Chipata cha Milu ya Phulusa. Iye anachimanga ndi kuika zitseko zake, akapichi ake ndi mipiringidzo yake.

15 Saluni mwana wamwamuna wa Kolihoze, kalonga wa chigawo cha Mizipa,+ anakonza Chipata cha Kukasupe.+ Iye anachimanga ndi kukhoma denga* lake. Anaikanso zitseko zake,+ akapichi ake ndi mipiringidzo yake. Iye anamanganso mpanda wa Dziwe+ la Ngalande* kukafika ku Munda wa Mfumu+ ndi ku Masitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide.+

16 Ndiyeno Nehemiya mwana wamwamuna wa Azibuki, kalonga wa hafu ya chigawo cha Beti-zuri,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Saluni analekezera, kukafika patsogolo pa Manda Achifumu+ a Davide* ndi kudziwe+ lochita kukumba, mpaka kukafikanso ku Nyumba ya Anthu Amphamvu.+

17 Ndiyeno Alevi,+ moyang’aniridwa ndi Rehumu mwana wamwamuna wa Bani,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Nehemiya analekezera. Hasabiya, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila,+ anakonza mpanda kuimira chigawo chake kuchokera pamene Alevi analekezera. 18 Abale awo anakonza mpandawo kuchokera pamenepo moyang’aniridwa ndi Bavai mwana wamwamuna wa Henadadi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila.

19 Ndiyeno Ezeri mwana wamwamuna wa Yesuwa,+ kalonga wa Mizipa,+ anakonza gawo lina la mpandawo pafupi ndi chikweza chimene anthu amadutsa popita Kosungira Zida pa Mchirikizo wa Khoma.+

20 Kenako, Baruki mwana wamwamuna wa Zabai,+ anagwira ntchito mwachangu kwambiri+ ndi kukonza gawo lina la mpandawo, kuchokera pa Mchirikizo wa Khoma kukafika pachipata cha nyumba ya Eliyasibu+ mkulu wa ansembe.

21 Kenako, Meremoti mwana wamwamuna wa Uliya,+ mwana wamwamuna wa Hakozi, anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera pachipata cha nyumba ya Eliyasibu mpaka polekezera nyumbayo.

22 Ndiyeno ansembe, amuna a ku Chigawo* cha Yorodano+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. 23 Kenako, Benjamini ndi Hasubu anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yawo kuchokera pamene ansembe analekezera. Kenako, Azariya mwana wamwamuna wa Maaseya, mwana wamwamuna wa Ananiya, anakonza mpandawo pafupi ndi nyumba yake kuchokera pamene Benjamini ndi Hasubu analekezera. 24 Kenako, Binui mwana wamwamuna wa Henadadi anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera panyumba ya Azariya kukafika ku Mchirikizo wa Khoma+ ndi kukona ya mpanda wa mzindawo.

25 Ndiyeno Palali mwana wamwamuna wa Uzai, anakonza mpandawo kutsogolo kwa Mchirikizo wa Khoma ndipo anakonzanso nsanja yochokera pa Nyumba ya Mfumu+ imene ili kumtunda m’Bwalo la Alonda.+ Kenako, Pedaya mwana wamwamuna wa Parosi,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Palali analekezera.

26 Anetini+ anali kukhala ku Ofeli.+ Iwonso anakonza mpandawo mpaka kukafika ku Chipata cha Kumadzi,+ kum’mawa. Iwo anakonzanso nsanja yotundumukira kunja kwa mpanda.

27 Kenako, Atekowa+ anakonza chigawo chinanso cha mpandawo, kuchokera patsogolo pa nsanja yaikulu yotundumukira kunja kwa mpanda ija mpaka kukafika kumpanda wa Ofeli.

28 Ansembe anakonza mpandawo kuyambira kumtunda kwa Chipata cha Hatchi,+ ndipo aliyense anali kukonza patsogolo pa nyumba yake.

29 Kenako, Zadoki+ mwana wamwamuna wa Imeri, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake.

Ndiyeno, Semaya mwana wamwamuna wa Sekaniya, woyang’anira Chipata cha Kum’mawa,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Zadoki analekezera.

30 Hananiya mwana wamwamuna wa Selemiya ndi Hanuni mwana wamwamuna wa 6 wa Zalafi, anakonzanso chigawo china cha mpanda.

Kenako Mesulamu+ mwana wamwamuna wa Berekiya, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba* yake kuchokera pamene winayo analekezera.+

31 Malikiya amene anali m’gulu la osula golide,+ anakonza mpandawo mpaka kukafika kunyumba ya Anetini+ ndi amalonda,+ kutsogolo kwa Chipata cha Kufufuza* mpaka pachipinda chapadenga cha pakona.

32 Ndiyeno osula golide ndi amalonda anakonza mpandawo kuyambira pachipinda chapadenga cha pakona kukafika pa Chipata cha Nkhosa.+

4 Tsopano Sanibalati+ atangomva kuti tinali kumanganso mpanda, anakhumudwa ndi kukwiya kwambiri,+ ndipo anali kunyoza+ Ayuda. 2 Iye anayamba kuuza abale ake+ ndi gulu lankhondo la ku Samariya kuti: “Kodi Ayuda ofookawa akuchita chiyani? Kodi akuona ngati akwanitsa chintchito chomanga chimenechi? Kodi adzapereka nsembe?+ Kodi amaliza kumangako tsiku limodzi? Kodi adzachita kufukula miyala imene inatenthedwa ndi kuigwiritsiranso ntchito?”+

3 Tsopano Tobia+ Muamoni,+ anali pamodzi ndi Sanibalati ndipo anati: “Ngakhaletu nkhandwe+ itakwera pampanda wamiyala umene akumangawo ingathe kuugwetsa ndithu.”

4 Ndiyeno Nehemiya anati: “Inu Mulungu wathu, imvani+ mawu onyoza amene akutinenera.+ Bwezerani chitonzo chawocho+ pamutu pawo ndipo apititseni m’dziko laukapolo monga zofunkha. 5 Musanyalanyaze cholakwa chawo+ ndi machimo amene anakuchitirani. Musawafafanizire machimowo chifukwa akhumudwitsa anthu omanga mpandawo.”

6 Choncho tinapitiriza kumanga mpandawo, ndipo khoma lonse linalumikizana mpaka kufika hafu ya kutalika kwake. Anthu anapitiriza kukhala ndi mtima wogwira ntchito.+

7 Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia,+ Aluya,+ Aamoni+ ndi Aasidodi+ atamva kuti ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu ikupita patsogolo, pakuti malo ogumuka anali atayamba kutsekedwa, anakwiya kwambiri. 8 Choncho onsewa anayamba kukonza chiwembu+ kuti abwere kudzamenyana ndi Yerusalemu ndi kudzatisokoneza. 9 Koma tinapemphera+ kwa Mulungu wathu, ndipo chifukwa cha adani amenewa, tinaika alonda kuti azititeteza usana ndi usiku.

10 Ndiyeno anthu a ku Yuda anayamba kunena kuti: “Mphamvu za anthu onyamula katundu+ zatha, koma pali zinyalala zambiri zofunika kuchotsa,+ ndipo ife sitingathe kumanga mpandawu tokha.”

11 Komanso adani athu anali kunena kuti: “Sadzadziwa+ kapena kuona kuti tikubwera, kufikira titafika pakati pawo ndipo tidzawapha ndithu ndi kuimitsa ntchito yomangayo.”

12 Ndiyeno pamene Ayuda okhala pafupi ndi adani amenewo anabwera anatiuza maulendo okwana 10 kuti: “Adaniwo adzabwera kumene ife tikukhala, kumenenso inu mudzabwera, ndipo adzatiukira kuchokera kumbali zonse.”

13 Choncho ndinaika amuna kuseli kwa mpanda pamalo otsika ndiponso oonekera. Ndinaikanso anthu onyamula malupanga,+ mikondo ing’onoing’ono+ ndi mauta malinga ndi mabanja awo. 14 Nditaona kuti akuchita mantha, nthawi yomweyo ndinanyamuka ndi kuuza anthu olemekezeka,+ atsogoleri+ ndi anthu onse kuti: “Musachite nawo mantha+ anthu amenewa. Kumbukirani Yehova, Mulungu wamkulu+ ndi wochititsa mantha.+ Menyerani nkhondo abale anu,+ ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”

15 Tsopano adani athuwo anamva kuti tadziwa za chiwembu chawo, mwakuti Mulungu woona anasokoneza cholinga chawo.+ Zitatero tonse tinabwerera ku ntchito yomanga mpanda, aliyense pa ntchito yake. 16 Kuchokera pamene adaniwo anamva kuti chiwembu chawo chadziwika mpaka m’tsogolo, hafu ya anyamata anga+ inali kalikiliki pa ntchito ndipo hafu yotsalayo inali kunyamula mikondo ing’onoing’ono, zishango, mauta ndipo inali kuvala zovala za mamba achitsulo.+ Ndipo akalonga+ anali kuima kumbuyo kwa Ayuda ndi kumawachirikiza. 17 Koma omanga mpandawo ndi anthu amene anali kunyamula katundu wolemera, aliyense wa iwo anali kalikiliki kugwira ntchito ndi dzanja limodzi ndipo kudzanja lina+ anali kunyamula mkondo.+ 18 Aliyense wa omangawo anali atamangirira lupanga lake m’chiuno+ pamene anali kumanga+ mpandawo, ndipo munthu woliza lipenga la nyanga ya nkhosa+ anali pambali panga.

19 Ndiyeno ndinauza anthu olemekezeka, atsogoleri+ ndi anthu ena onse kuti: “Ntchito yakula kwambiri ndipo tamwazikana kuzungulira mpandawu. 20 Mukamva kwina kukulira lipenga la nyanga ya nkhosa, musonkhane kumeneko, ndipo ife tidzakhala tili kumeneko. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”+

21 Pamene hafu ya amunawo inali kalikiliki kugwira ntchito, hafu ina inali kunyamula mikondo ing’onoing’ono kuyambira m’bandakucha mpaka usiku nyenyezi zitatuluka. 22 Kuwonjezera apo, pa nthawiyo ndinauza anthu kuti: “Mwamuna aliyense pamodzi ndi mtumiki wake azigona mu Yerusalemu,+ ndipo usiku azikhala alonda athu koma masana azigwira ntchito.” 23 Koma ine,+ abale anga,+ atumiki anga+ ndi amuna olondera+ amene anali pambuyo panga, sitinali kuvula zovala zathu, ndipo aliyense anali ndi mkondo+ m’dzanja lake lamanja.

5 Tsopano amuna ena pamodzi ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri+ ndipo anali kutsutsana ndi abale awo achiyuda.+ 2 Ena anali kunena kuti: “Tikumapereka ana athu aamuna ndi ana athu aakazi monga chikole kuti tipeze chakudya ndi kukhala ndi moyo.”+ 3 Ndipo ena anali kunena kuti: “Nthawi ya njala, tikumapereka minda yathu ya tirigu, minda yathu ya mpesa ndi nyumba zathu monga chikole+ kuti tipeze chakudya.” 4 Enanso anali kunena kuti: “Ife takongola ndalama kuti tikhome msonkho kwa mfumu+ wa minda yathu ya tirigu ndi minda yathu ya mpesa.+ 5 Komatu ife ndi anzathuwo ndife pachibale.+ Ana athu aamuna n’chimodzimodzi ndi ana awo aamuna, koma ife tikusandutsa ana athu aamuna ndi ana athu aakazi kukhala akapolo.+ Ndipotu ena mwa ana athu aakazi tawasandutsa kale akapolo. Ife tilibenso mphamvu, chifukwa minda yathu ya tirigu ndi minda yathu ya mpesa ili m’manja mwa anthu ena.”

6 Pamenepo ine ndinakwiya kwambiri nditangomva kudandaula kwawo komanso mawu amenewa. 7 Choncho ndinayamba kuganiza mumtima mwanga ndipo ndinapeza kuti anthu olemekezeka ndi atsogoleri anali olakwa.+ Pamenepo ndinawauza kuti: “Nonsenu mukuumiriza abale anu kukupatsani chiwongoladzanja chokwera kwambiri.”+

Kenako ndinaitanitsa msonkhano waukulu chifukwa cha iwowa.+ 8 Ndipo ndinawauza kuti: “Ife tachita zonse zimene tikanatha mwa kuwombola+ abale athu achiyuda amene anagulitsidwa kwa anthu a mitundu ina. Kodi pa nthawi imodzimodziyo inu mukugulitsa abale anu,+ ndipo kodi ife tiwawombole?” Pamenepo anangokhala chete, kusowa chonena.+ 9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+ 10 Ndiponso ine, abale anga ndi atumiki anga, tikukongoza ndalama ndi chakudya kwa abale athu. Chonde, tiyeni tileke kulandira chiwongoladzanja tikakongoza zinthu.+ 11 Chonde, lero abwezereni minda yawo ya tirigu,+ minda yawo ya mpesa, minda yawo ya maolivi, nyumba zawo ndi limodzi mwa magawo 100 a ndalama, tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta zimene munalandira kwa iwo monga chiwongoladzanja.”

12 Pamenepo iwo anati: “Tiwabwezera,+ ndipo sitiwaumirizanso kuti atipatse kena kalikonse.+ Tichita ndendende mmene wanenera.”+ Choncho ndinaitana ansembe ndi kulumbiritsa olakwawo kuti achite mogwirizana ndi mawu amenewa.+ 13 Kuwonjezera apo, ndinakutumula zovala zanga, kenako ndinati: “Mofanana ndi zimenezi, Mulungu woona akutumule munthu aliyense wosachita mogwirizana ndi mawu amenewa, kum’chotsa m’nyumba yake ndi pa zinthu zake zonse. Ndipo munthu wotero akutumulidwe mwa njira imeneyi ndi kukhala wopanda kalikonse.” Pamenepo mpingo wonse unati: “Zikhale momwemo!”*+ Ndipo anayamba kutamanda Yehova.+ Choncho anthuwo anachitadi mogwirizana ndi mawu amenewa.+

14 Chinanso: Kwa zaka 12, kuchokera tsiku limene anandiika kukhala bwanamkubwa wawo+ m’dziko la Yuda, m’chaka cha 20+ mpaka m’chaka cha 32+ cha mfumu Aritasasita,+ ine ndi abale anga sitinadye chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa.+ 15 Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu, ndipo tsiku ndi tsiku anali kulandira masekeli* 40 a siliva kuti akagule chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo anali kupondereza anthu.+ Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+

16 Kuwonjezera apo, ndinagwira nawo ntchito yomanga mpandawo+ ndipo sitinakhale ndi minda.+ Atumiki anga onse anasonkhana pamodzi kumeneko kuti agwire ntchito. 17 Ayuda ndi atsogoleri, amuna okwana 150, pamodzi ndi anthu obwera kwa ife kuchokera ku mitundu yotizungulira anali kudya nafe limodzi.+ 18 Tsiku lililonse ndinali kuuza anthu kuti akonze ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa zosankhidwa mwapadera 6 ndi mbalame. Ndipo kamodzi pa masiku 10 alionse ndinali kupereka vinyo wochuluka wamtundu uliwonse.+ Kuwonjezera pamenepo, sindinapemphe kuti andipatse chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa chifukwa utumiki umene anthuwa anali kuchita unali wolemetsa. 19 Mulungu wanga, mundikumbukire+ pa zabwino+ zonse zimene ndachitira anthu awa.+

6 Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia,+ Gesemu+ Mluya+ ndi adani athu onse atangouzidwa kuti ndamanganso mpanda,+ ndipo palibe mpata umene watsala (ngakhale kuti kufikira pa nthawiyo ndinali ndisanaike zitseko+ m’zipata zake),+ 2 nthawi yomweyo Sanibalati ndi Gesemu ananditumizira uthenga wakuti: “Tiye tipangane nthawi kuti tikumane+ m’mudzi wina wa m’chigwa cha Ono.”+ Koma anali kundikonzera chiwembu.+ 3 Choncho ndinawatumizira amithenga+ kuti akawauze kuti: “Ntchito imene ndikugwirayi ndi yaikulu,+ sindingathe kupita kumeneko. Kodi ntchitoyi iime chifukwa chakuti ine ndabwera kwa inu?”+ 4 Koma iwo ananditumizira uthenga wofananawo maulendo anayi, ndipo ine ndinali kuwayankha chimodzimodzi.

5 Kenako Sanibalati+ ananditumizira uthenga wofananawo ulendo wachisanu kudzera mwa mtumiki wake. Mtumikiyo anali ndi kalata yosatseka m’manja mwake. 6 M’kalatayo analemba kuti: “Zamveka pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ N’chifukwa chake iwe ukumanga mpandawo, ndipo malinga ndi zimene zikumvekazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo.+ 7 Komanso waika aneneri kuti azilengeza za iwe mu Yerusalemu monse kuti, ‘Dziko la Yuda lili ndi mfumu!’ Ife tikanena zinthu zimenezi kwa mfumu. Choncho bwera tikambirane.”+

8 Koma ine ndinamutumizira uthenga wonena kuti: “Palibe amene wachita zimene ukunenazi,+ koma wangozipeka mumtima mwako.”+ 9 Onsewo anali kungofuna kutichititsa mantha, ndipo anali kunena kuti: “Manja awo+ adzalefuka ndipo adzasiya kugwira ntchitoyi, mwakuti siitha.” Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.+

10 Ndiyeno ine ndinalowa m’nyumba ya Semaya mwana wamwamuna wa Delaya, mwana wamwamuna wa Mehetabele, amene anali atadzitsekera m’nyumba.+ Iye anandiuza kuti: “Tipangane nthawi kuti tikakumane+ kunyumba ya Mulungu woona, m’kachisi,+ ndi kutseka zitseko za kachisiyo, pakuti akubwera kudzakupha, ngakhale usiku+ akubwera ndithu kudzakupha.” 11 Koma ine ndinati: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe?+ Kodi munthu ngati ine angalowe m’kachisi ndi kukhala ndi moyo?+ Ine sindikalowamo!” 12 Nditafufuza ndinapeza kuti sanatumidwe ndi Mulungu,+ koma Tobia ndi Sanibalati+ anamulemba ganyu+ kuti andinenere+ ulosi woipa umenewu. 13 Iwo anamulemba ganyu+ n’cholinga choti ndichite mantha+ kuti ndikalowe m’kachisi ndi kuchimwa.+ Mwakutero, akanandiipitsira dzina langa+ kuti azindinyoza.+

14 Inu Mulungu wanga, kumbukirani+ zinthu zonse zimene Tobia+ ndi Sanibalati anachita. Mukumbukirenso Nowadiya mneneri wamkazi+ ndi aneneri ena onse amene anali kuyesetsabe kundiopseza.

15 Patapita nthawi, ntchito yomanga mpanda+ inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli.* Ntchitoyi inatenga masiku 52.

16 Ndiyeno adani athu onse atangomva zimenezi,+ komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi ndipo anadziwa kuti ntchito imeneyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu.+ 17 Komanso masiku amenewo, anthu olemekezeka+ a mu Yuda anali kulemberana makalata ambiri ndi Tobia.+ 18 Pakuti anthu ambiri mu Yuda anamulumbirira kukhala naye mwamtendere chifukwa anali mkamwini wa Sekaniya, mwana wamwamuna wa Ara.+ Ndipo Yehohanani mwana wamwamuna wa Tobia, anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu,+ mwana wamwamuna wa Berekiya. 19 Komanso anthu amenewa anali kunena zinthu zabwino za Tobia pamaso panga nthawi zonse.+ Anthuwo anali kutenga zimene ine ndanena ndi kukauza Tobia. Ndipo Tobia anali kundilembera makalata ondiopseza.+

7 Ndiyeno mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika alonda a m’zipata,+ oimba+ ndi Alevi.+ 2 Zitatero ndinaika Haneni+ m’bale wanga ndi Hananiya kalonga wa m’Nyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyang’anira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika+ ndipo anali woopa kwambiri+ Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri. 3 Choncho ndinawauza kuti: “Zipata+ za Yerusalemu siziyenera kutsegulidwa kufikira dzuwa litatentha. Alonda a m’zipatazo atseke zitseko ndi kuzikhoma ndi akapichi ndipo aime pafupi.+ Muikenso alonda a anthu okhala mu Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.”+ 4 Tsopano mzindawo unali wotakasuka ndi waukulu. Mkati mwake munali anthu ochepa+ ndipo sanamangemo nyumba.

5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga+ kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina awo motsatira mzere wawo wobadwira.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina a mzere wobadwira+ wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti m’bukumo analembamo izi:

6 Awa ndi anthu a m’chigawo+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatengera ku ukapolo ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ 7 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya,* Raamiya,* Nahamani, Moredekai,+ Bilisani, Misiperete,* Bigivai, Nehumu,* ndi Bana.

Chiwerengero cha amuna a Isiraeli ndi ichi: 8 Ana a Parosi,+ 2,172. 9 Ana a Sefatiya,+ 372. 10 Ana a Ara,+ 652. 11 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818. 12 Ana a Elamu,+ 1,254. 13 Ana a Zatu,+ 845. 14 Ana a Zakai,+ 760. 15 Ana a Binui,+ 648. 16 Ana a Bebai,+ 628. 17 Ana a Azigadi,+ 2,322. 18 Ana a Adonikamu,+ 667. 19 Ana a Bigivai,+ 2,067. 20 Ana a Adini,+ 655. 21 Ana a Ateri,+ a m’nyumba ya Hezekiya, 98. 22 Ana a Hasumu,+ 328. 23 Ana a Bezai,+ 324. 24 Ana a Harifi,+ 112. 25 Ana a Gibeoni,+ 95. 26 Amuna a ku Betelehemu+ ndi ku Netofa,+ 188. 27 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 28 Amuna a ku Beti-azimaveti,+ 42. 29 Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira,+ ndi ku Beeroti,+ 743. 30 Amuna a ku Rama+ ndi ku Geba,+ 621. 31 Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 32 Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123. 33 Amuna a ku Nebo wina,+ 52. 34 Ana a Elamu wina,+ 1,254. 35 Ana a Harimu,+ 320. 36 Ana a Yeriko,+ 345. 37 Ana a Lodi,+ Hadidi+ ndi Ono,+ 721. 38 Ana a Senaya,+ 3,930.

39 Ansembe: Ana a Yedaya,+ a m’nyumba ya Yesuwa, 973. 40 Ana a Imeri,+ 1,052. 41 Ana a Pasuri,+ 1,247. 42 Ana a Harimu,+ 1,017.

43 Alevi: Ana a Yesuwa, a m’nyumba ya Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva,+ 74. 44 Oimba,+ ana a Asafu,+ 148. 45 Alonda a pachipata,+ ana a Salumu,+ ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita, ana a Sobai,+ 138.

46 Anetini:+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,+ 47 ana a Kerosi, ana a Siya,* ana a Padoni,+ 48 ana a Lebana, ana a Hagaba,+ ana a Salimai, 49 ana a Hanani,+ ana a Gideli, ana a Gahara, 50 ana a Reyaya,+ ana a Rezini,+ ana a Nekoda, 51 ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya, 52 ana a Besai,+ ana a Meyuni, ana a Nefusesimu,*+ 53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,+ 54 ana a Baziliti,* ana a Mehida, ana a Harisa,+ 55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,+ 56 ana a Neziya, ana a Hatifa.+

57 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,*+ 58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,+ 59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu, ana a Amoni.*+ 60 Anetini onse+ pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.

61 Ndiyeno amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri,+ ndipo sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, kuti kaya anali ochokera mu Isiraeli kapena ayi, ndi awa: 62 ana a Delaya, ana a Tobia, ana a Nekoda,+ 642. 63 Ansembe+ anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ana a Barizilai+ amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ Mgiliyadi ndipo anayamba kutchedwa ndi dzina lawo. 64 Amenewa ndiwo anayang’ana mayina awo m’kaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanawapeze.+ Zitatero anawaletsa kuti asatumikire monga ansembe chifukwa anali oipitsidwa.+ 65 Pa chifukwa chimenechi, Tirisata*+ anawauza kuti sayenera kudya+ zinthu zopatulika koposa kufikira patakhala wansembe wokhala ndi Urimu+ ndi Tumimu.+

66 Mpingo wonsewo monga gulu limodzi unali ndi anthu 42,360,+ 67 kupatulapo akapolo awo aamuna+ ndi akapolo awo aakazi amene analipo 7,337.+ Iwo analinso ndi oimba aamuna+ ndi aakazi+ 245. 68 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245.+ 69 Ngamila+ zinalipo 435. Abulu analipo 6,720.+

70 Ndiye panali atsogoleri+ ena a nyumba za makolo+ amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchito.+ Tirisata+ anapereka ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zikuluzikulu 50, ndi mikanjo ya ansembe 530 kumalo osungira chuma.+ 71 Ndiyeno panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200.+ 72 Zimene anthu ena onse anapereka zinakwana ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67.

73 Ndiyeno ansembe,+ Alevi, alonda a pazipata, oimba,+ anthu ena onse pamodzi ndi Anetini+ ndi Isiraeli yense anapita kukakhala m’mizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7+ ana a Isiraeli anali atakhala m’mizinda yawo.+

8 Ndiyeno anthu onse anasonkhana pamodzi mogwirizana+ m’bwalo lalikulu+ limene linali pafupi ndi Chipata cha Kumadzi.+ Pamenepo anthuwo anauza Ezara+ wokopera Malemba kuti abweretse buku+ la chilamulo cha Mose+ limene Yehova analamula Aisiraeli kuti azilitsatira.+ 2 Choncho Ezara wansembe+ anabweretsa chilamulo pamaso pa mpingo+ wa amuna komanso akazi ndi ana onse amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira+ zimene zinali kunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+ 3 Ezara anawerenga+ mokweza bukulo m’bwalo lalikulu limene linali pafupi ndi Chipata cha Kumadzi, kuyambira m’mawa+ mpaka masana. Anali kuwerenga bukuli pamaso pa amuna, akazi ndi ana amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira. Anthu onse anatchera khutu kuti amve+ zimene zinali m’buku la chilamuloli. 4 Ezara wokopera Malembayo, anaimirira pansanja yamatabwa+ imene inamangidwa chifukwa cha mwambo umenewu. Pafupi naye, kudzanja lake lamanja kunaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya, ndi Maaseya. Ndipo kudzanja lake lamanzere kunaimirira Pedaya, Misayeli, Malikiya,+ Hasumu,+ Hasi-badana, Zekariya ndi Mesulamu.

5 Ndiyeno Ezara anatsegula+ bukulo pamaso pa anthu onse, pakuti iye anaimirira pamalo okwera kusiyana ndi anthu onse. Pamene iye anali kutsegula bukulo anthu onse anaimirira.+ 6 Kenako Ezara anatamanda Yehova+ Mulungu woona, Mulungu wamkulu. Atatero anthu onse anakweza manja awo m’mwamba+ ndi kuyankha kuti, “Ame! Ame!”*+ Ndiyeno anthuwo anagwada+ ndi kuwerama pamaso pa Yehova mpaka nkhope zawo pansi.+ 7 Pamenepo Alevi anali kufotokozera anthu chilamulocho,+ anthuwo ataimirira.+ Alevi amenewo anali Yesuwa, Bani, Serebiya,+ Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi,+ Hanani ndi Pelaya.+ 8 Iwo anapitiriza kuwerenga+ bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokozera ndi kumveketsa tanthauzo lake. Iwo anapitiriza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerenga.+

9 Ndiyeno Nehemiya+ amene ndiye Tirisata+ komanso Ezara+ wansembe, wokopera Malemba, ndi Alevi amene anali kupereka malangizo kwa anthu, anauza anthuwo kuti: “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musakhale achisoni ndipo musalire.”+ Ananena zimenezi chifukwa anthu onse anali kulira pamene anali kumvetsera mawu a m’chilamulo.+ 10 Nehemiya anapitiriza kunena kuti: “Pitani mukadye zinthu zonona, kumwa zinthu zokoma ndi kugawa chakudya+ kwa anthu amene sanathe kudzikonzera chakudya, pakuti lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Choncho musadzimvere chisoni pakuti chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.” 11 Ndiyeno Alevi anali kuuza anthu onse kuti akhale chete ndipo anati: “Khalani chete! pakuti lero ndi tsiku lopatulika, musadzimvere chisoni.” 12 Choncho anthu onse anapita kukadya, kukamwa, kukagawira ena chakudya+ ndi kukondwera kwambiri+ chifukwa anamvetsa bwino mawu amene anawafotokozera.+

13 Tsiku lachiwiri, atsogoleri a mabanja a anthu onse komanso ansembe ndi Alevi, anasonkhana pamodzi pamaso pa Ezara wokopera Malemba, kuti amvetse bwino mawu a m’chilamulo.+ 14 Pamenepo anapeza kuti m’chilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose+ analembamo kuti ana a Isiraeli azikhala m’misasa+ pa nthawi ya chikondwerero m’mwezi wa 7.+ 15 Analembamonso kuti azilengeza+ ndi kufuula m’mizinda yonse ndi mu Yerusalemu monse+ kuti: “Pitani kumapiri+ mukatenge nthambi za mitengo ya maolivi,+ nthambi za mitengo ya mafuta, nthambi za mitengo ya mchisu, masamba akanjedza ndi nthambi za mitengo ya masamba ambiri kuti mudzapangire misasa mogwirizana ndi zolembedwa.”

16 Pamenepo anthu anatuluka ndi kukatenga zinthu zimenezi ndipo anapangira misasa. Aliyense anapanga msasa pamwamba pa nyumba yake+ komanso m’mabwalo awo, m’mabwalo+ a nyumba ya Mulungu woona, m’bwalo lalikulu+ la Chipata cha Kumadzi+ ndiponso m’bwalo lalikulu la Chipata cha Efuraimu.+ 17 Choncho mpingo wonse wa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa ndi kukhala m’misasayo. Panali chisangalalo chachikulu kwambiri+ chifukwa chakuti ana a Isiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera m’masiku a Yoswa mwana wa Nuni,+ mpaka kudzafika tsiku limeneli. 18 Ndiyeno tsiku ndi tsiku, kuchokera tsiku loyamba mpaka tsiku lomaliza, anali kuwerenga mokweza buku la chilamulo cha Mulungu woona.+ Iwo anachita chikondwererocho masiku 7, ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera malinga ndi lamulo.+

9 Pa tsiku la 24 la mwezi umenewu+ ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi. Iwo anali kusala kudya+ atavala ziguduli*+ ndiponso atadzithira dothi+ kumutu. 2 Pamenepo mbewu ya Isiraeli inadzipatula+ kwa anthu onse osakhala Aisiraeli.+ Atatero anaimirira ndi kuulula+ machimo awo+ ndi zolakwa za makolo awo.+ 3 Iwo anaimirira pomwepo+ ndipo anawerenga mokweza buku la chilamulo+ cha Yehova Mulungu wawo kwa maola atatu.*+ Kwa maola enanso atatu anali kuulula machimo awo+ ndi kugwadira Yehova Mulungu wawo.+

4 Ndiyeno Yesuwa, Bani, Kadimiyeli, Sebaniya,+ Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani anakwera pansanja+ ya Alevi ndi kuyamba kufuula kwa Yehova Mulungu wawo ndi mawu amphamvu.+ 5 Choncho Yesuwa, Kadimiyeli, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya, omwe anali Alevi, anati: “Dzukani, tamandani+ Yehova Mulungu wanu kuyambira kalekale mpaka kalekale.*+ Inu Mulungu wathu, anthuwa atamande dzina lanu laulemerero,+ lokwezeka kuposa dalitso ndi chitamando chilichonse.

6 “Inu ndinu Yehova, inu nokha.+ Ndinu amene munapanga kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba ndi makamu ake onse.+ Ndinu amene munapanga dziko lapansi+ ndi zonse zili momwemo+ komanso nyanja+ ndi zonse zili momwemo.+ Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu+ akumwamba amakugwadirani. 7 Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu+ ndi kum’tulutsa ku Uri wa Akasidi+ ndipo munamutcha dzina lakuti Abulahamu.+ 8 Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika pamaso panu.+ Chotero munachita naye pangano+ kuti mudzam’patsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Munachita naye pangano kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbewu yake,+ ndipo munachitadi zimene munanena chifukwa ndinu wolungama.+

9 “Choncho inu munaona+ nsautso ya makolo athu ku Iguputo ndipo munamvanso kulira kwawo pa Nyanja Yofiira.+ 10 Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikiro ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake.+ Munatero chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangira dzina+ kufikira lero. 11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+ 12 Usana munali kuwatsogolera ndi mtambo woima njo ngati chipilala,+ ndipo usiku munali kuwatsogolera ndi moto woima njo ngati chipilala+ kuti uziwaunikira+ njira imene anayenera kuyendamo. 13 Ndiyeno munatsikira paphiri la Sinai+ ndi kulankhula nawo muli kumwamba.+ Munawapatsa zigamulo zowongoka+ ndi malamulo a choonadi,+ mfundo zabwino ndi malangizo abwino.+ 14 Munawaphunzitsa za sabata lanu lopatulika.+ Munawapatsa malangizo, mfundo ndi chilamulo kudzera mwa Mose mtumiki wanu.+ 15 Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+

16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu. 17 Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+ 18 Pamene anasungunula chitsulo n’kudzipangira chifanizo cha mwana wa ng’ombe+ n’kuyamba kunena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mu Iguputo,’+ ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani, 19 inuyo simunawasiye m’chipululu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Mtambo woima njo ngati chipilala sunawachokere usana ndipo unali kuwatsogolera,+ ngakhalenso moto woima njo ngati chipilala sunawachokere usiku ndipo unali kuwaunikira njira imene anayenera kuyendamo.+ 20 Munawapatsa mzimu wanu wabwino+ kuti akhale anzeru. Simunawamane mana+ ndipo munawapatsa madzi kuti athetse ludzu lawo.+ 21 Kwa zaka 40+ munawapatsa chakudya m’chipululu. Iwo sanasowe kanthu.+ Zovala zawo sizinathe+ ndipo mapazi awo sanatupe.+

22 “Pamenepo munawapatsa maufumu+ ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo chigawo ndi chigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ dziko la mfumu ya Hesiboni+ ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana.+ 23 Ndipo munawachulukitsira ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Mutatero munawalowetsa m’dziko+ limene munalonjeza makolo awo+ kuti akalowe ndi kulitenga. 24 Choncho ana awo+ analowa ndi kutenga dzikolo,+ ndipo munagonjetsa+ anthu okhala m’dzikolo, Akanani,+ ndi kuwapereka m’manja mwawo. Munaperekanso ngakhale mafumu a Akananiwo+ ndi mitundu ya anthu ya m’dzikolo+ kwa ana a Isiraeliwo kuti awachite zimene akufuna.+ 25 Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Analandanso nthaka yachonde,+ nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino,+ zitsime,*+ minda ya mpesa ndi ya maolivi+ ndi mitengo ya zipatso yochuluka. Atatero, anayamba kudya, kukhuta,+ kunenepa+ ndi kukondwera ndi ubwino wanu waukulu.+

26 “Koma iwo anakhala osamvera+ ndipo anakupandukirani.+ Anapitiriza kufulatira chilamulo chanu,+ ndipo anapha aneneri anu+ amene anali kuwalimbikitsa kuti abwerere kwa inu.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+ 27 Chifukwa chochita zimenezi, munawapereka m’manja mwa adani awo+ amene anapitiriza kuwasautsa.+ Koma akakumana ndi nsautso, anali kukulirirani,+ ndipo inu munali kumva muli kumwambako.+ Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu,+ munali kuwapatsa owapulumutsa+ amene anali kuwalanditsa m’manja mwa adani awo.+

28 “Koma akangokhala pa mtendere, anali kuchitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munali kuwasiya m’manja mwa adani awo amene anali kuwapondaponda.+ Zikatero, anali kubweranso kwa inu ndi kupempha thandizo lanu,+ ndipo inu munali kumva muli kumwambako+ ndi kuwapulumutsa mobwerezabwereza, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+ 30 Koma munaleza nawo mtima kwa zaka zambiri+ ndipo munapitirizabe kuwachenjeza+ mwa mzimu wanu potumiza aneneri anu, koma iwo sanamvere.+ Pamapeto pake munawapereka m’manja mwa mitundu ya anthu ya m’dzikolo.+ 31 Koma mwachifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya,+ pakuti inu ndinu Mulungu wachisomo+ ndi wachifundo.+

32 “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu,+ wamphamvu+ ndi wochititsa mantha,+ wosunga pangano+ ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha,+ musachepetse+ mavuto onse amene agwera ifeyo,+ mafumu athu,+ akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu+ ndi anthu anu onse kuchokera masiku a mafumu a Asuri mpaka lero.+ 33 Inu ndinu wolungama+ pa zinthu zonse zimene zatichitikira, pakuti inu mwachita zinthu mokhulupirika+ koma ife tachita zinthu zoipa.+ 34 Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu+ sanatsatire chilamulo chanu+ ndipo sanamvere malamulo anu+ kapena zikumbutso zanu zowachenjeza.+ 35 Iwo sanakutumikireni+ ndipo sanabwerere kusiya zoipa zimene anali kuchita+ pamene anali ndi mafumu+ komanso pamene munali kuwapatsa zabwino zochuluka,+ m’dziko lalikulu ndi lachonde+ limene munawapatsa. 36 Onani, lero ife ndife akapolo.+ Ndife akapolo m’dziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino.+ 37 Zokolola za m’dzikoli zachulukira+ mafumu+ amene mwatiikira chifukwa cha machimo athu.+ Iwo akulamulira matupi athu komanso ziweto zathu mmene akufunira, ndipo tili pamavuto aakulu.+

38 “Choncho chifukwa cha zimenezi, tikuchita pangano lodalirika+ ndi kulilemba, ndipo akalonga athu, Alevi athu ndi ansembe athu akutsimikizira panganoli ndi chidindo chawo.”+

10 Tsopano amene anatsimikizira panganoli ndi chidindo+ chawo ndi awa:

Nehemiya+ amene ndiye Tirisata,+ mwana wa Hakaliya,+

Komanso Zedekiya, 2 Seraya,+ Azariya, Yeremiya, 3 Pasuri, Amariya, Malikiya, 4 Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5 Harimu,+ Meremoti, Obadiya, 6 Danieli,+ Ginetoni, Baruki, 7 Mesulamu, Abiya, Miyamini, 8 Maaziya, Biligai ndi Semaya. Amenewa anali ansembe.

9 Panalinso Alevi awa amene anatsimikizira panganoli: Yesuwa,+ mwana wamwamuna wa Azaniya, Binui wochokera pakati pa ana a Henadadi,+ Kadimiyeli, 10 ndi abale awo awa, Sebaniya,+ Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11 Mika, Rehobu, Hasabiya, 12 Zakuri, Serebiya,+ Sebaniya, 13 Hodiya, Bani ndi Beninu.

14 Atsogoleri awa a anthu anatsimikiziranso panganoli: Parosi, Pahati-mowabu,+ Elamu, Zatu, Bani, 15 Buni, Azigadi, Bebai, 16 Adoniya,* Bigivai, Adini, 17 Ateri, Hezekiya, Azuri, 18 Hodiya, Hasumu, Bezai, 19 Harifi,* Anatoti, Nebai, 20 Magipiasi, Mesulamu, Heziri, 21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22 Pelatiya, Hanani, Anaya, 23 Hoshiya, Hananiya, Hasubu, 24 Halohesi, Pila, Sobeki, 25 Rehumu, Hasabina, Maaseya, 26 Ahiya, Hanani, Anane, 27 Maluki, Harimu ndi Bana.

28 Ndiyeno anthu ena onse, ansembe,+ Alevi,+ alonda a pazipata,+ oimba,+ Anetini,+ ndi aliyense amene anadzipatula kwa mitundu ya anthu a m’mayikowo+ kuti asunge chilamulo+ cha Mulungu woona, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi ndi aliyense wodziwa zinthu ndi wozindikira,+ 29 anali kumamatirabe kwa abale awo,+ anthu otchuka.+ Iwo anali kudzilowetsa m’lumbiro limene likanatha kuwabweretsera temberero.+ Lumbiro+ limenelo linali lakuti tidzatsatira chilamulo cha Mulungu woona+ chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu woona, ndi kusunga+ malamulo onse, zigamulo ndi mfundo+ za Yehova Ambuye wathu,+ 30 kutinso tisapereke ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu ya m’dzikoli, ndiponso tisatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana athu aamuna.+

31 Kunena za mitundu ya anthu a m’dzikolo+ imene inali kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse* pa sabata, tinalumbira kuti sitigula kalikonse kuchokera kwa iwo pa sabata+ kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitiyenera kulima minda yathu m’chaka cha 7,+ ndipo tiyenera kukhululukira ngongole wina aliyense.+

32 Kuwonjezera apo, tinadziikira malamulo akuti chaka chilichonse aliyense wa ife azipereka gawo limodzi mwa magawo atatu a sekeli kuti ndalama zimenezo akazigwiritsire ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsire ntchito pokonza mkate wosanjikiza,+ nsembe yachikhalire yambewu,+ nsembe yachikhalire yopsereza ya pa tsiku la sabata+ ndi tsiku lokhala mwezi.+ Akazigwiritsirenso ntchito pokonza madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika+ ndi nsembe yamachimo+ yophimbira machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse za panyumba ya Mulungu wathu.+

34 Komanso tinachita maere+ okhudza ansembe, Alevi ndi anthu oti azibweretsa nkhuni+ kunyumba ya Mulungu wathu, mogwirizana ndi nyumba ya makolo athu, pa nthawi zoikidwiratu, chaka ndi chaka kuti aziziyatsira moto paguwa lansembe la Yehova Mulungu wathu,+ malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo.+ 35 Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+ 36 Kutinso azibweretsa ana aamuna oyamba kubadwa+ mwa ana athu ndi ziweto+ zathu malinga ndi zolembedwa m’chilamulo.+ Komanso kuti azibweretsa ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi nkhosa+ zathu kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene anali kutumikira m’nyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tinafunika kupititsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu,+ zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano+ ndi mafuta+ kwa ansembe kumalo odyera+ m’nyumba ya Mulungu wathu. Tinafunikanso kupititsa chakhumi kwa Alevi+ pa zinthu zochokera m’nthaka yathu, pakuti Aleviwo anali kulandira chakhumi kuchokera m’mizinda yathu yonse ya zaulimi.

38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akulandira chakhumi.* Aleviwo azipereka gawo limodzi mwa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu+ wathu kuzipinda zodyera+ m’nyumba yosungiramo zinthu. 39 Pakuti ana a Isiraeli ndi ana a Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta kuzipinda zodyera. Kumeneku ndi kumene kuli ziwiya za kumalo opatulika ndi ansembe amene anali kutumikira,+ olondera pazipata+ ndi oimba,+ ndipo tisanyalanyaze nyumba ya Mulungu wathu.+

11 Tsopano akalonga+ a anthuwo anali kukhala m’Yerusalemu.+ Anthu ena onse anachita maere+ kuti apeze munthu mmodzi mwa anthu 10 alionse woti akakhale m’Yerusalemu, mzinda woyera,+ ndiponso kuti anthu ena 9 otsalawo akhale m’mizinda ina. 2 Komanso, anthu anadalitsa+ amuna onse amene anadzipereka+ kukakhala m’Yerusalemu.

3 Otsatirawa ndiwo atsogoleri a m’chigawo cha Yuda+ amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ koma m’mizinda ya Yuda munali kukhala ansembe,+ Alevi,+ Anetini+ ndi ana a atumiki a Solomo.+ Aliyense wa iwo anali kukhala m’malo ake m’mizinda yawo+ mu Isiraeli.+

4 Mu Yerusalemu munalinso kukhala ena mwa ana a Yuda ndi ena mwa ana a Benjamini.+ Mwa ana a Yuda panali Ataya mwana wamwamuna wa Uziya amene anali mwana wa Zekariya. Zekariya anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Sefatiya, Sefatiya anali mwana wa Mahalalele wochokera m’banja la Perezi.+ 5 Panalinso Maaseya mwana wa Baruki amene anali mwana wa Kolihoze. Kolihoze anali mwana wa Hazaya, Hazaya anali mwana wa Adaya, Adaya anali mwana wa Yoyaribi, Yoyaribi anali mwana wa Zekariya amene anali mwana wa Mshela. 6 Ana onse a Perezi amene anali kukhala mu Yerusalemu anali amuna amphamvu zawo okwana 468.

7 Ana aamuna a Benjamini+ anali awa: Salelu mwana wa Mesulamu,+ Mesulamu anali mwana wa Yoedi, Yoedi anali mwana wa Pedaya, Pedaya anali mwana wa Kolaya, Kolaya anali mwana wa Maaseya, Maaseya anali mwana wa Itiyeli, ndipo Itiyeli anali mwana wa Yesaiya. 8 Pambuyo pa Salelu panali Gabai ndi Salai ndipo onse pamodzi analipo 928. 9 Yoweli mwana wa Zikiri anali woyang’anira wawo ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali wachiwiri kwa woyang’anira mzinda.

10 Pakati pa ansembe panali awa: Yedaya mwana wa Yoyaribi,+ Yakini,+ 11 Seraya mwana wa Hilikiya, Hilikiya anali mwana wa Mesulamu,+ Mesulamu anali mwana wa Zadoki,+ Zadoki anali mwana wa Merayoti, Merayoti anali mwana wa Ahitubu.+ Ahitubu anali mtsogoleri wa panyumba ya Mulungu woona. 12 Abale awo ogwira ntchito panyumbapo+ analipo 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu.+ Yerohamu anali mwana wa Pelaliya, Pelaliya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Pasuri,+ ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya.+ 13 Abale ake a Adaya, atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ analipo 242. Ndiyeno panalinso Amasisai mwana wa Azareli. Azareli anali mwana wa Azai, Azai anali mwana wa Mesilemoti amene anali mwana wa Imeri. 14 Amasisai pamodzi ndi abale ake, amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ analipo okwana 128. Iwowa mtsogoleri+ wawo anali Zabidiyeli wochokera m’banja la anthu otchuka.

15 Pakati pa Alevi+ panali awa: Semaya mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, Azirikamu anali mwana wa Hasabiya,+ ndipo Hasabiya anali mwana wa Buni. 16 Panalinso Sabetai+ ndi Yozabadi,+ mwa atsogoleri a Alevi. Amenewa anali kuyang’anira ntchito ya panja pa nyumba ya Mulungu woona. 17 Mataniya+ mwana wa Mika amene anali mwana wa Zabidi mwana wa Asafu,+ anali wotsogolera nyimbo zotamanda+ Mulungu. Iye anali kutamanda Mulungu pa nthawi ya mapemphero.+ Bakibukiya anali wachiwiri kwa woyang’anira pakati pa abale ake. Panalinso Abada mwana wa Samuwa, Samuwa anali mwana wa Galali, ndipo Galali+ anali mwana wa Yedutuni.+ 18 Alevi onse mumzinda woyera+ analipo 284.

19 Alonda a pazipata+ anali Akubu, Talimoni,+ ndi abale awo amene anali kulondera m’zipata.+ Onse pamodzi analipo 172.

20 Aisiraeli ena onse, komanso ansembe ndi Alevi ena onse, anali m’mizinda ina ya Yuda, aliyense pacholowa chake.+ 21 Anetini+ anali kukhala ku Ofeli,+ ndipo Ziha ndi Gisipa anali kuyang’anira Anetiniwo.

22 Woyang’anira+ Alevi pa ntchito ya panyumba ya Mulungu woona mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani. Bani anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Mataniya,+ Mataniya anali mwana wa Mika+ wa m’banja la Asafu.+ A m’banja la Asafu anali oimba.+ 23 Mfumu inapereka lamulo lokhudza oimba,+ ndipo panali dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse malinga ndi zofunikira za tsikulo.+ 24 Petahiya mwana wa Mesezabele, wa m’banja la Zera mwana wa Yuda, anali wothandiza mfumu pa nkhani zonse zokhudza anthu.

25 Ana ena a Yuda anali kukhala m’midzi ndi m’madera ozungulira midziyo.+ Ena anali kukhala ku Kiriyati-ariba+ ndi midzi yake yozungulira, ku Diboni* ndi midzi yake yozungulira, ku Yekabizeeli+ ndi midzi yake yozungulira, 26 ku Yesuwa, ku Molada,+ ku Beti-peleti,+ 27 ku Hazara-suali,+ ku Beere-seba+ ndi midzi yake yozungulira, 28 ku Zikilaga,+ ku Mekona ndi midzi yake yozungulira, 29 ku Eni-rimoni,+ ku Zora,+ ku Yarimuti,+ 30 ku Zanowa,+ ku Adulamu+ ndi midzi yake yozungulira, ku Lakisi+ ndi madera ake ozungulira, ku Azeka+ ndi midzi yake yozungulira. Iwo anamanga misasa kuyambira ku Beere-seba mpaka kuchigwa cha Hinomu.+

31 Ana a Benjamini anakhala ku Geba,+ Mikimasi,+ Aiya,+ Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, 32 ku Anatoti,+ Nobu,+ Ananiya, 33 Hazori, Rama,+ Gitaimu,+ 34 Hadidi, Zeboyimu, Nebalati, 35 Lodi,+ Ono+ ndi kuchigwa cha amisiri. 36 Ndipo ena mwa Alevi a ku Yuda anakakhala ku Benjamini.

12 Otsatirawa anali ansembe ndi Alevi amene anapita ndi Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa:+ Seraya, Yeremiya, Ezara, 2 Amariya,+ Maluki, Hatusi, 3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti, 4 Ido, Ginetoi, Abiya, 5 Miyamini, Maadiya, Biliga, 6 Semaya,+ Yoyaribi, Yedaya,+ 7 Salelu,* Amoki,+ Hilikiya ndi Yedaya.+ Amenewa ndiwo anali atsogoleri a ansembe komanso a abale awo m’masiku a Yesuwa.+

8 Ndiyeno panali Alevi awa: Yesuwa,+ Binui,+ Kadimiyeli,+ Serebiya, Yuda ndi Mataniya.+ Mataniya ndi abale akewa anali oyang’anira oimba nyimbo zoyamika Mulungu. 9 Bakibukiya ndi Uni amene ndi abale awo, anaima moyang’anizana nawo kuti azigwira ntchito ya ulonda. 10 Yesuwa anabereka Yoyakimu,+ Yoyakimu anabereka Eliyasibu,+ Eliyasibu anabereka Yoyada.+ 11 Yoyada anabereka Yonatani, Yonatani anabereka Yaduwa.+

12 M’masiku a Yoyakimu kunali ansembe awa, atsogoleri a nyumba za makolo:+ woimira nyumba ya Seraya+ anali Meraya, woimira nyumba ya Yeremiya anali Hananiya. 13 Woimira nyumba ya Ezara+ anali Mesulamu, woimira nyumba ya Amariya anali Yehohanani. 14 Woimira nyumba ya Maluka anali Yonatani, woimira nyumba ya Sebaniya+ anali Yosefe. 15 Woimira nyumba ya Harimu+ anali Adena, woimira nyumba ya Merayoti anali Helikai. 16 Woimira nyumba ya Ido anali Zekariya, woimira nyumba ya Ginetoni anali Mesulamu. 17 Woimira nyumba ya Abiya+ anali Zikiri, woimira nyumba ya Miniyamini* anali . . . ,* woimira nyumba ya Moadiya anali Pilitai. 18 Woimira nyumba ya Biliga+ anali Samuwa, woimira nyumba ya Semaya anali Yehonatani. 19 Woimira nyumba ya Yoyaribi anali Matenai, woimira nyumba ya Yedaya+ anali Uzi. 20 Woimira nyumba ya Salai anali Kalai, woimira nyumba ya Amoki anali Ebere. 21 Woimira nyumba ya Hilikiya anali Hasabiya ndipo woimira nyumba ya Yedaya+ anali Netaneli.

22 M’masiku a Eliyasibu,+ Yoyada,+ Yohanani ndi Yaduwa,+ mayina a Alevi komanso ansembe anali kuwalemba m’gulu la atsogoleri a nyumba za makolo mpaka kudzafika m’nthawi ya ufumu wa Dariyo Mperisiya.

23 Mayina a ana aamuna a Levi, monga atsogoleri a nyumba za makolo,+ analembedwa m’buku la zochitika pa nthawi imeneyo mpaka kudzafika m’masiku a Yohanani, mwana wa Eliyasibu. 24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya+ ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo anaima moyang’anizana nawo kuti azitamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi lamulo+ la Davide, munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda. 25 Mataniya,+ Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu+ anali kulondera monga alonda a m’zipata.+ Amenewa anali kulondera pafupi ndi zipinda zosungiramo zinthu m’zipata za kachisi. 26 Anthu amenewa anakhalapo m’masiku a Yoyakimu+ mwana wa Yesuwa+ amene anali mwana wa Yozadaki,+ komanso m’masiku a Nehemiya+ amene anali bwanamkubwa, ndi Ezara+ amene anali wansembe komanso wokopera Malemba.+

27 Ndiyeno mwambo wotsegulira+ mpanda wa Yerusalemu uli pafupi kuchitika, anthu anafunafuna Alevi m’malo awo onse ndi kubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala ndi kuyamika+ Mulungu mwa kuimba nyimbo+ pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe+ ndi azeze.+ 28 Ana aamuna a oimbawo anasonkhana pamodzi kuchokera m’Chigawo*+ chapafupi, m’madera onse ozungulira Yerusalemu komanso m’midzi yonse kumene Anetofa anali kukhala.+ 29 Ena anachokera ku Beti-giligala+ komanso m’dera la Geba+ ndi la Azimaveti,+ pakuti kumeneko kunali midzi+ imene oimba anamanga kuzungulira Yerusalemu yense. 30 Ndiyeno ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ ndi kuyeretsanso anthu,+ zipata+ ndi khoma la mpandawo.+

31 Kenako ine ndinabwera ndi akalonga+ a Yuda pampandawo. Komanso ndinaika magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika+ Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu limodzi la oimba linali kuyenda pampandawo kudzanja lamanja molunjika Chipata cha Milu ya Phulusa.+ 32 Hoshaya ndi hafu ya akalonga a Yuda anayamba kuyenda pambuyo pa oimbawo, 33 komanso Azariya, Ezara, Mesulamu, 34 Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. 35 Mwa ana a ansembe oimba malipenga+ panalinso Zekariya mwana wa Yonatani. Yonatani anali mwana wa Semaya, Semaya anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali mwana wa Mikaya, Mikaya anali mwana wa Zakuri,+ ndipo Zakuri anali mwana wa Asafu.+ 36 Panalinso Semaya, Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, Yuda ndi Haneni, abale ake a Zekariya. Amenewa anali ndi zipangizo+ zoimbira za Davide, munthu wa Mulungu woona, ndipo Ezara+ wokopera Malemba ndiye anali kuwatsogolera. 37 Oimbawo atafika pa Chipata cha Kukasupe,+ gulu lowatsatira lija lili pambuyo pawo, anayenda pamalo okwera a mpandawo kudutsa pa Masitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide+ mpaka kukafika kumtunda kwa Nyumba ya Davide. Kenako anafika ku Chipata cha Kumadzi,+ kum’mawa kwa chipatacho.

38 Gulu lina loimba nyimbo zoyamika+ Mulungu linali kuyenda patsogolo, ndipo ine ndinali pambuyo pawo pamodzi ndi hafu ya anthuwo. Oimbawo anayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 39 Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda.

40 Kenako magulu awiri oimba nyimbo zoyamikawo+ anafika panyumba+ ya Mulungu woona. Ine pamodzi ndi atsogoleri amene ndinali nawo tinafikanso komweko.+ 41 Kunafikanso ansembe otsatirawa okhala ndi malipenga:+ Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, Hananiya, 42 Maaseya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezeri. Ndipo oimba pamodzi ndi Izirahiya woyang’anira wawo anali kuimba mokweza.+

43 Pa tsiku limenelo anapereka nsembe zochuluka+ ndipo anasangalala+ pakuti Mulungu woona anawachititsa kusangalala kwambiri.+ Akazi+ ndi ana+ nawonso anasangalala, mwakuti phokoso la chisangalalo cha Yerusalemu linamveka kutali.+

44 Kuwonjezera apo, pa tsiku limenelo anaika amuna kuti aziyang’anira zipinda+ zosungiramo zinthu zosiyanasiyana,+ zopereka,+ mbewu zoyambirira+ ndi chakhumi.+ Anawapatsa udindo wosonkhanitsira m’zipindamo gawo loyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ malinga ndi chilamulo,+ kuchokera m’minda yonse ya m’mizinda yawo. Yuda anali kusangalala chifukwa ansembe ndi Alevi+ anali kuchita utumiki wawo. 45 Choncho ansembe ndi Alevi pamodzi ndi oimba+ ndi alonda a pazipata+ anayamba kusamalira udindo+ wawo kwa Mulungu ndi kusunga lamulo lakuti azikhala oyera,+ malinga ndi lamulo la Davide ndi mwana wake Solomo. 46 Kalelo m’masiku a Davide ndi Asafu, kunali atsogoleri a oimba nyimbo+ ndipo anthu anali kuimba nyimbo zotamanda ndi kuyamika Mulungu.+ 47 Aisiraeli onse m’masiku a Zerubabele+ komanso m’masiku a Nehemiya+ anali kupereka gawo loyenera kwa oimba+ ndi alonda a pachipata+ malinga ndi zofunikira zawo za tsiku ndi tsiku. Ndipo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa Alevi.+ Aleviwo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa ana a Aroni.

13 Pa tsiku limenelo buku+ la Mose linawerengedwa+ pamaso pa anthuwo. Iwo anapeza kuti m’bukumo analembamo kuti Muamoni+ ndi Mmowabu+ aliyense sayenera kubwera mumpingo wa Mulungu woona mpaka kalekale,+ 2 chifukwa iwowa sanachingamire ana a Isiraeli kuti awapatse chakudya+ ndi madzi.+ M’malomwake, analemba ganyu Balamu+ kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+ 3 Choncho atangomva chilamulocho,+ anayamba kupatula+ khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana kuwachotsa pakati pa Isiraeli.

4 Zimenezi zisanachitike, panali Eliyasibu+ wansembe amene anali kuyang’anira zipinda zodyeramo+ m’nyumba ya Mulungu wathu, ndipo anali wachibale wa Tobia.+ 5 Eliyasibu anakonzera Tobia chipinda chachikulu chodyeramo+ m’chipinda chimene nthawi zonse anali kuikamo nsembe yambewu,+ lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda a pazipata anayenera kulandira, komanso zimene anali kupereka kwa ansembe.

6 Nthawi yonseyi ine sindinali mu Yerusalemu, pakuti m’chaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke.+ 7 Ndiyeno ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinaona zoipa zimene Eliyasibu+ anachita mwa kukonzera Tobia+ chipinda m’bwalo la nyumba+ ya Mulungu woona. 8 Zimenezi zinandiipira kwambiri.+ Choncho, katundu yense wa m’nyumba ya Tobia ndinam’ponyera kunja+ kwa chipinda chodyeramo. 9 Zitatero ndinalamula kuti ayeretse+ zipinda zodyeramo+ ndipo anachitadi zomwezo. Kenako ndinabwezera pamalo pake ziwiya+ za nyumba ya Mulungu woona pamodzi ndi zopereka zambewu ndi lubani.+

10 Ndiyeno ndinazindikira kuti magawo+ a Alevi sanali kuperekedwa kwa iwo, moti aliyense wa Aleviwo ndi oimba amene anali kutumikira anathawa ndipo anapita kumunda wake.+ 11 Zitatero ndinayamba kuimba mlandu+ atsogoleriwo+ ndi kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani nyumba ya Mulungu woona yasiyidwa chonchi?”+ Pamenepo ndinawasonkhanitsa pamodzi ndipo ndinawaika pamalo awo ogwirira ntchito. 12 Anthu onse a mu Yuda anabweretsa kumalo osungira zinthu+ chakhumi+ cha mbewu,+ cha vinyo watsopano+ ndiponso cha mafuta.+ 13 Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba ndi Pedaya mmodzi mwa Alevi, kuti akhale oyang’anira malo osungira zinthu. Amenewa anali kuyang’anira Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya,+ pakuti anthu anali kuwaona kuti ndi okhulupirika.+ Iwowa anapatsidwa udindo wogawa+ zinthu kwa abale awo.

14 Mundikumbukire,+ inu Mulungu wanga, chifukwa cha zinthu zimenezi ndipo musaiwale+ ntchito za kukoma mtima kosatha zimene ndachitira nyumba+ ya Mulungu wanga ndi onse otumikira kumeneko.

15 Masiku amenewo ku Yuda ndinaona anthu akuponda moponderamo mphesa tsiku la sabata.+ Anali kubweretsa mbewu ndi kuzikweza+ pa abulu.+ Analinso kukweza pa abuluwo vinyo, mphesa, nkhuyu+ ndi katundu wosiyanasiyana ndipo anali kubwera nazo ku Yerusalemu tsiku la sabata.+ Ine ndinawadzudzula pa tsiku limene anali kugulitsa zinthu zimenezi. 16 Anthu a ku Turo+ anali kukhala mumzindawo ndipo anali kubweretsa nsomba ndi malonda osiyanasiyana.+ Iwo anali kugulitsa zinthu zimenezi pa tsiku la sabata kwa ana a Yuda mu Yerusalemu. 17 Choncho ndinayamba kuimba mlandu anthu olemekezeka+ a ku Yuda kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita zinthu zoipa, mpaka kuipitsa tsiku la sabata? 18 Kodi izi si zimene makolo anu anachita,+ mwakuti Mulungu wathu anadzetsa tsoka lonseli+ pa ife komanso pamzinda uwu? Koma inu mukuwonjezera kuyaka kwa mkwiyo wake pa Isiraeli mwa kuipitsa sabata.”+

19 Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+ 20 Choncho ochita malonda ndi ogulitsa zinthu zosiyanasiyana anagona panja pa Yerusalemu kawiri. 21 Pamenepo ndinawachenjeza+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukugona kunja kwa mpanda? Mukachitanso zimenezi ndikukhaulitsani.”+ Kuyambira nthawi imeneyo sanabwerenso pa tsiku la sabata.

22 Ndiyeno ndinauza Alevi+ kuti pobwera azidziyeretsa nthawi zonse+ komanso azilondera zipata za mzinda+ kuti tsiku la sabata likhale loyera.+ Inu Mulungu wanga, mundikumbukirenso+ pa zimenezi ndipo mundimvere chifundo malinga ndi kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

23 Komanso ndinaona kuti Ayuda ena anali atakwatira+ akazi achiasidodi,+ achiamoni ndi achimowabu.+ 24 Hafu ya ana awo aamuna anali kulankhula Chiasidodi ndipo palibe amene ankatha kulankhula Chiyuda,+ koma anali kulankhula chinenero cha anthu ena. 25 Ndiyeno ndinayamba kuwaimba mlandu ndi kuwatemberera.+ Ena mwa amuna amenewo ndinawamenya,+ kuwazula tsitsi ndi kuwalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti:+ “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+ 26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli?+ Mwa mitundu yonse panalibe mfumu yofanana naye.+ Iye anakondedwa ndi Mulungu wake,+ mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi achilendo anamuchimwitsa.+ 27 Kodi si zodabwitsa kuti inunso mukuchita choipa chachikulu chimenechi, mwa kukwatira akazi achilendo, kumene ndi kuchita mosakhulupirika kwa Mulungu wanu?”+

28 Ndiyeno mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni.+ Choncho ndinamuthamangitsa, kum’chotsa pamaso panga.+

29 Inu Mulungu wanga, akumbukireni amenewa chifukwa anaipitsa+ unsembe ndiponso pangano+ limene munachita ndi ansembe ndi Alevi.+

30 Ndiyeno ndinawayeretsa+ mwa kuchotsa chilichonse chachilendo. Ndinapereka ntchito kwa ansembe ndi Alevi, aliyense ndinam’patsa ntchito yake,+ 31 ngakhale ntchito yobweretsa nkhuni+ pa nthawi zoikidwiratu ndi mbewu zoyamba kucha.

Inu Mulungu wanga, mundikumbukire+ pa zabwino zimene ndinachita.+

Dzinali limatanthauza “Ya Amatonthoza; Ya Ndi Chitonthozo.”

Onani Zakumapeto 13.

N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Yuda.

Onani Zakumapeto 13.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Mwina amenewa anali malo amene anali kutchedwanso kuti Chitsime cha Eni-rogeli.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Kapena kuti “tsindwi.”

Kapena kuti “Dziwe la Sela.”

Zikuoneka kuti amenewa ndi manda a Davide ndi mafumu a Yuda amene anabwera pambuyo pake.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

Kapena kuti “chipinda chachikulu.”

Kapena kuti “Chipata cha Hamifikadi.”

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Onani Zakumapeto 13.

Pa Eza 2:2 akutchedwa “Seraya.”

Pa Eza 2:2 akutchedwa “Reelaya.”

Pa Eza 2:2 akutchedwa “Misipara.”

Pa Eza 2:2 akutchedwa “Rehumu.”

Pa Eza 2:44 akutchedwa “Siyaha.”

Pa Eza 2:50 akutchedwa “Nefusimu.”

Pa Eza 2:52 akutchedwa “Baziluti.”

Pa Eza 2:55 akutchedwa “Peruda.”

Pa Eza 2:57 akutchedwa “Ami.”

Onani mawu a m’munsi pa Eza 2:63.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Onani mawu a m’munsi pa Eza 2:69.

Onani Zakumapeto 12.

Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”

Ena amati “masaka.”

Mawu ake enieni, “gawo lachinayi la tsiku.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “phewa laliuma.”

Zikuoneka kuti ameneyu ndi Adonikamu wotchulidwa pa Eza 2:13.

Zikuoneka kuti ameneyu ndi Hasumu wotchulidwa pa Eza 2:19.

Zimenezi mwina zinali tirigu kapena barele.

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Zikuoneka kuti malowa ndi amodzimodzi ndi “Dimona” wotchulidwa pa Yos 15:22.

Zikuoneka kuti ameneyu ndi Salai wotchulidwa m’vesi 20.

Mu vesi 5 akutchedwa “Miyamini.”

Zikuoneka kuti m’Malemba Achiheberi sanam’tchule dzina.

N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Yorodano.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena