Esitere
1 M’masiku a Ahasiwero,*+ amene anali kulamulira zigawo 127 monga mfumu, kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya,+ 2 m’masiku amenewo mfumuyo inali kulamulira ili m’nyumba yachifumu+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri+ ya ku Susani.+ 3 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, Ahasiwero anakonzera phwando+ akalonga ndi atumiki ake onse, akuluakulu a asilikali a Perisiya+ ndi Mediya,+ anthu olemekezeka+ ndi akalonga a m’zigawo za ufumu wake.+ 4 Masiku amenewo, iye anaonetsa anthuwo chuma+ chimene chinali kuchititsa anthu kumupatsa ulemu+ ndi ulemerero mu ufumu wake, komanso anawaonetsa kukongola kwa ufumu wakewo. Anawaonetsa zimenezi kwa masiku ambiri, masiku okwana 180. 5 Masiku amenewa atatha, mfumu inakonza phwando la masiku 7 m’munda wamaluwa, pabwalo la nyumba yake. Phwandoli inakonzera anthu onse okhala kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani, anthu olemekezeka ndi anthu wamba omwe. 6 Anapachika makatani a nsalu, makatani opangidwa ndi thonje labwino kwambiri ndi makatani abuluu.+ Makataniwo anawamanga ndi zingwe zopangidwa ndi nsalu zabwino kwambiri ndi zingwe zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira.+ Zingwezi anazikulunga pamikombero yasiliva ndi pazipilala za miyala ya mabo. Anazikulunganso pamipando+ yagolide ndi siliva yokhala ngati mabedi. Mipandoyi inali pakhonde la miyala ya pofeli,* miyala yoyera ya mabo, ngale ndi miyala yakuda ya mabo.
7 Anthu anali kulandira vinyo m’ziwiya zagolide.+ Chiwiya chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake, ndipo vinyo amene mfumu inapereka+ anali wochuluka kwambiri, moti ndi mfumu yokha imene ikanatha kupereka vinyo wochuluka choncho. 8 Pa nthawiyo, palibe amene anali kuwakakamiza kutsatira malamulo a kamwedwe, pakuti umu ndi mmene mfumu inakonzera kuti aliyense wogwira ntchito kunyumba ya mfumu amwe mmene akufunira.
9 Nayonso Mfumukazi Vasiti+ inakonzera phwando akazi kunyumba ya Mfumu Ahasiwero.
10 Pa tsiku la 7, pamene mtima wa mfumu unali kukondwera ndi vinyo,+ mfumu inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 za panyumba ya mfumu zimene zinali kutumikira+ Mfumu Ahasiwero, 11 kuti abweretse Mfumukazi Vasiti itavala duku lachifumu pamaso pa mfumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kuoneka bwino kwake, pakuti inalidi yokongola kwambiri.+ 12 Koma Mfumukazi Vasiti inakana+ kubwera itaitanidwa ndi mfumu kudzera mwa nduna za panyumba ya mfumu. Pamenepo mfumu inakwiya kwambiri ndipo mumtima mwake munali ukali waukulu.+
13 Ndiyeno mfumu inalankhula ndi amuna anzeru,+ odziwa miyambo ya masiku amenewo.+ (Pakuti pa nkhani iliyonse, mfumu inali kufunsira kwa onse odziwa malamulo ndi nkhani zokhudzana ndi milandu. 14 Alangizi amene anali pafupi kwambiri ndi mfumu anali Karisena, Setara, Adimata, Tarisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, akalonga 7+ a Perisiya ndi Mediya, amene nthawi zonse anali kufika pamaso pa mfumu+ komanso anali ndi maudindo akuluakulu mu ufumuwo.) 15 Choncho mfumu inawafunsa kuti: “Popeza Mfumukazi Vasiti siinachite zimene Mfumu Ahasiwero yanena kudzera mwa nduna zake, kodi tichite nayo chiyani malinga ndi malamulo?”
16 Pamenepo Memukani+ anayankha pamaso pa mfumu ndi akalonga kuti: “Mfumukazi Vasiti siinalakwire mfumu yokha,+ koma yalakwiranso akalonga onse ndi anthu a mitundu yonse a m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti zimene mfumukazi yachita zidziwika kwa akazi onse okwatiwa ndipo iwo ayamba kunyoza+ amuna awo+ ponena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero inalamula kuti Mfumukazi Vasiti ibwere pamaso pake koma Vasiti sanapite.’ 18 Lero akazi a akalonga a Perisiya ndi Mediya amene amva zimene mfumukazi yachita alankhula chimodzimodzi ndi akalonga onse a mfumu ndipo pakhala kunyozana ndi kukwiyitsana.+ 19 Ngati zingakukomereni mfumu,+ lamulani monga mfumu ndipo lamuloli alilembe m’malamulo+ a Perisiya ndi Mediya kuti zimene mwalamula zisasinthe.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke ulemu wake wachifumu kwa mkazi wina, mkazi wabwino kuposa iyeyu. 20 Lamulo limene inu mfumu mupereke limveke mu ufumu wanu wonse (chifukwa ndi waukulu), ndipo akazi onse okwatiwa adzalemekeza+ amuna awo,+ kaya amunawo ndi olemekezeka kapena anthu wamba.”
21 Mawu amenewa anali osangalatsa kwa mfumu+ ndi akalonga, ndipo mfumu inachita mogwirizana ndi mawu a Memukani. 22 Choncho mfumu inalemba makalata ndi kuwatumiza+ m’zigawo zonse za ufumu wake. Chigawo chilichonse+ anachilembera kalata malinga ndi mmene anthu a kumeneko amalembera ndiponso malinga ndi chinenero chawo. Anachita izi kuti mwamuna aliyense apitirize kutsogolera banja lake monga mutu,+ ndiponso kuti banjalo lizilankhula chinenero cha anthu a mtundu wa mwamunayo.
2 Pambuyo pake, mkwiyo wa Mfumu Ahasiwero+ utachepa, iye anakumbukira Vasiti+ ndi zimene anachita,+ komanso chilango chimene anasankha kum’patsa.+ 2 Ndiyeno atumiki a mfumu, amene anali nduna zake,+ anati: “Pakhale anthu oti afufuzire+ mfumu atsikana, anamwali+ okongola. 3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu m’zigawo zonse+ za ufumu wanu. Anthuwo asonkhanitse pamodzi atsikana onse, anamwali okongola, kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ m’nyumba ya akazi imene Hegai+ akuyang’anira. Iye ndi munthu wofulidwa wa mfumu+ woyang’anira akazi, amenenso ndi mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa. 4 Mtsikana amene mtima wanu mfumu udzakondwere naye adzakhala mfumukazi m’malo mwa Vasiti.”+ Mawu amenewa anasangalatsa mfumu, ndipo inachitadi zomwezo.
5 Tsopano mwamuna wina, Myuda, anali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Mwamunayu dzina lake anali Moredekai+ mwana wa Yairi, mwana wa Simeyi amene anali mwana wa Kisi M’benjamini.+ 6 Moredekai anali atatengedwa ku Yerusalemu pamodzi ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+ Anthuwa ndi amene anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anam’tenga kupita naye ku ukapolo. 7 Moredekai ndi amene analera+ Hadasa, amene ndi Esitere, mwana wa m’bale wa bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndi wokongola kwambiri.+ Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredekai anam’tenga ngati mwana wake. 8 Ndiyeno mawu a mfumu ndi malamulo ake atamveka, komanso atsikana ambiri atawasonkhanitsa pamodzi kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani+ kuti Hegai+ aziwayang’anira, Esitere nayenso anam’tengera kunyumba ya mfumu komweko kuti Hegai woyang’anira akazi azimuyang’anira.
9 Tsopano Hegai anasangalala naye mtsikanayu moti anam’sonyeza kukoma mtima kosatha.+ Mwamsanga anam’paka mafuta okongoletsa,+ anam’patsa chakudya chapadera ndiponso anam’patsa atsikana 7 osankhidwa kuchokera kunyumba ya mfumu. Kenako anam’samutsa pamodzi ndi atsikanawo n’kuwapatsa malo abwino kwambiri m’nyumba ya akaziyo. 10 Esitere sananene za mtundu wa anthu ake+ kapena za abale ake, pakuti Moredekai anali atamulamula kuti asanene kalikonse.+ 11 Ndipo tsiku lililonse Moredekai anali kuyenda m’bwalo la nyumba ya akazi kuti adziwe mmene Esitere anali kukhalira ndi zimene zinali kum’chitikira.
12 Mtsikana aliyense anali kukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero pambuyo poti am’chitira zonse zimene amayenera kum’chitira pa miyezi 12 malinga ndi lamulo lokhudza akazi. Atsikanawo anali kuwapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako anali kuwapaka mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ndiye kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera. 13 Zimenezi zikachitika, mtsikana aliyense anali kubwera kwa mfumu. Anali kum’patsa chilichonse chimene wapempha kuti atenge pochokera kunyumba ya akazi kupita kunyumba ya mfumu.+ 14 Madzulo mtsikanayo anali kubwera kwa mfumu, ndipo m’mawa anali kubwerera kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi anali kuyang’anira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu,+ mkulu woyang’anira akazi. Mtsikanayo sanalinso kubwera kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yakondwera naye ndipo yamuitanitsa mwa kum’tchula dzina.+
15 Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekere kwa mfumu, sanapemphe kalikonse+ kupatulapo zimene Hegai+ anatchula. Iye anali munthu wofulidwa wa mfumu woyang’anira akazi, amenenso anali mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Esitere anali mwana wa Abihaili, m’bale wa bambo ake a Moredekai, amene Moredekai anamutenga ngati mwana wake+ (pa nthawi imeneyi Esitere anali kukondedwa ndi aliyense womuona).+ 16 Pamenepo anatenga Esitere kupita naye kwa Mfumu Ahasiwero, kunyumba yake yachifumu, m’mwezi wa 10 umene ndi mwezi wa Tebeti,* m’chaka cha 7+ cha ulamuliro wa Mfumu Ahasiwero. 17 Ndiyeno mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti mfumu inakondwera naye ndipo inamusonyeza kukoma mtima kosatha kuposa anamwali ena onse.+ Pamenepo mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake ndi kumusandutsa mfumukazi+ m’malo mwa Vasiti. 18 Kenako mfumu inakonzera akalonga ake ndi atumiki ake onse phwando lalikulu, phwando la Esitere. Ndiyeno mfumu inamasula+ anthu m’madera ake onse, ndipo inali kupereka mphatso zimene mfumu yokha ndiyo ikanatha kupereka mphatso zoterozo.
19 Pamene anamwali+ anasonkhanitsidwa pamodzi kachiwiri, Moredekai anali atakhala pansi kuchipata cha mfumu.+ 20 Esitere sanali kunena za abale ake ndi anthu a mtundu wake,+ monga mmene Moredekai+ anamulamulira.+ Esitere anali kuchita zimene Moredekai wanena monga mmene anali kuchitira pa nthawi imene Moredekai anali kumusunga.+
21 M’masiku amenewo, pamene Moredekai anali kukhala pansi kuchipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri za panyumba ya mfumu, amenenso anali alonda a pakhomo, anakwiya ndipo anafuna kupha+ Mfumu Ahasiwero. 22 Ndiyeno zimenezi zinadziwika kwa Moredekai ndipo iye mofulumira anauza+ Mfumukazi Esitere. Kenako Esitere analankhula ndi mfumu m’malo mwa Moredekai.+ 23 Choncho nkhani imeneyi anaifufuza ndipo pamapeto pake zonse zinadziwika, ndipo onse awiri, Bigitana ndi Teresi anapachikidwa+ pamtengo.+ Kenako zimenezi zinalembedwa pamaso pa mfumu m’buku la zochitika+ za m’masiku amenewo.
3 Pambuyo pake, Mfumu Ahasiwero analemekeza Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ ndipo anam’kweza+ ndi kum’patsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse amene mfumuyo inali nawo.+ 2 Choncho atumiki onse a mfumu amene anali kuchipata cha mfumu+ anali kuwerama ndi kugwadira Hamani, pakuti mfumu inali italamula kuti anthu azim’chitira zimenezi. Koma Moredekai sanali kumuweramira kapena kumugwadira.+ 3 Ndiyeno atumiki a mfumu amene anali kuchipatako anayamba kufunsa Moredekai kuti: “N’chifukwa chiyani ukunyalanyaza lamulo la mfumu?”+ 4 Popeza kuti anali kulankhula naye tsiku ndi tsiku koma sanali kuwamvera, anthuwo anakauza Hamani kuti aone ngati Moredekai angapitirize zimene anali kuchitazo,+ pakuti anawauza kuti anali Myuda.+
5 Hamani anakwiya kwambiri+ chifukwa anaona kuti Moredekai sanali kumuweramira ndi kumugwadira.+ 6 Koma Hamani anaona kuti n’zosakwanira kupha Moredekai yekha pakuti anthu anamuuza za anthu a mtundu wa Moredekai. Choncho Hamani anayamba kufunafuna kufafaniza+ Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredekai amene anali mu ufumu wonse wa Ahasiwero.+
7 Ndiyeno m’mwezi woyamba,+ umene ndi mwezi wa Nisani,* m’chaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, munthu wina anachita Puri*+ kapena kuti Maere+ pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Choncho Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 8 Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu umene ukupezeka paliponse+ ndipo ukudzipatula pakati pa anthu m’zigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira+ malamulo anu mfumu. Choncho si bwino kuti inu mfumu muwalekerere anthu amenewa. 9 Ngati zingakukomereni mfumu, palembedwe makalata kuti anthu amenewa awonongedwe. Ine ndidzapereka matalente 10,000+ asiliva kwa anthu amene adzagwira ntchito imeneyi+ kuti abweretse matalentewo mosungiramo chuma cha mfumu.”
10 Pamenepo mfumu inavula mphete yodindira+ kudzanja lake ndi kuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ amene anali kudana kwambiri ndi Ayuda.+ 11 Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva+ akhale wako, pamodzinso ndi anthuwa ndipo uchite nawo zimene ukuona kuti n’zabwino.”+ 12 Kenako anaitana alembi a mfumu+ m’mwezi woyamba, pa tsiku la 13 la mweziwo. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a m’zigawo zosiyanasiyana+ za ufumuwo ndi akalonga a anthu osiyanasiyana m’chigawo chilichonse. Makalata amenewa anawalemba malinga ndi mmene anthu a m’chigawo chilichonse anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo. Makalatawa anawalemba m’dzina+ la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yake yodindira.+
13 Ndiyeno anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma+ kupita kuzigawo zonse za mfumu. Anachita izi kuti pa tsiku limodzi,+ pa tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ awononge, aphe ndi kufafaniza Ayuda onse, mnyamata komanso mwamuna wachikulire, ana ndi akazi ndi kufunkha zinthu zawo.+ 14 Zimene analemba m’makalatawo kuti zikhale lamulo+ kuzigawo zonse,+ anazifalitsa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15 Amtokomawo anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndi lamulo limene linaperekedwa m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Ndipo mfumu ndi Hamani, anakhala pansi kuti amwe vinyo,+ koma mumzinda wa Susani+ munali chipwirikiti.+
4 Moredekai+ anadziwa zonse zimene zinachitika.+ Choncho anang’amba zovala zake ndi kuvala chiguduli*+ ndipo anadzithira phulusa+ ndi kutuluka kupita pakati pa mzinda. Ndiyeno anayamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima.+ 2 Kenako anafika pafupi ndi chipata cha mfumu,+ pakuti palibe amene anali kuloledwa kufika pachipata cha mfumu atavala chiguduli. 3 Ndipo m’zigawo zonse,+ kulikonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, Ayuda anali ndi chisoni kwambiri+ ndipo anali kusala kudya,+ kubuma ndi kulira mofuula. Ambiri anayala ziguduli+ ndi kuwazapo phulusa+ kuti agonepo. 4 Ndiyeno atsikana otumikira Esitere ndi amuna ofulidwa+ amene anali kumuyang’anira anayamba kubwera kudzamuuza zimenezi. Ndipo mfumukaziyo inamva chisoni kwambiri, choncho inatumiza zovala kuti Moredekai akavule zigudulizo ndi kuvala zovalazo, koma Moredekai sanalole.+ 5 Pamenepo Esitere anaitana Hataki,+ mmodzi mwa amuna ofulidwa a mfumu amene mfumuyo inamuika kuti azitumikira Esitere. Ndiyeno anamutumiza kwa Moredekai kuti akafufuze zimene zachitika.
6 Choncho Hataki anapita kwa Moredekai kubwalo la mzinda limene linali pafupi ndi chipata cha mfumu. 7 Kenako Moredekai anauza Hataki zonse zimene zamuchitikira.+ Anamuuzanso zonse zokhudza ndalama zimene Hamani ananena kuti apereka mosungiramo chuma cha mfumu,+ n’cholinga chofuna kuwononga Ayuda.+ 8 Ndiyeno anapatsa Hataki kalata+ imene munali lamulo lochokera ku Susani+ lakuti Ayuda afafanizidwe. Anamupatsa kalata imeneyi kuti akaonetse Esitere ndi kumuuza+ kuti akaonekere kwa mfumu ndi kuipempha kuti iwakomere mtima,+ ndiponso kuti Esitere akachonderere mfumu mwachindunji m’malo mwa anthu a mtundu wake.+
9 Ndiyeno Hataki+ anapita kukauza Esitere mawu a Moredekai. 10 Kenako Esitere anauza Hataki kuti akauze Moredekai+ mawu akuti: 11 “Atumiki onse a mfumu ndi anthu a m’zigawo za mfumu akudziwa kuti mfumu ili ndi lamulo limodzi lokhudza mwamuna kapena mkazi aliyense wokaonekera kwa iye m’bwalo lamkati+ asanaitanidwe. Lamuloli+ ndi lakuti aphedwe. Koma ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yachifumu ya golide, pamenepo adzakhala ndi moyo.+ Ndiye ine sindinaitanidwe kukaonekera kwa mfumu kwa masiku 30 tsopano.”
12 Ndiyeno Moredekai anauzidwa mawu a Esitere. 13 Kenako Moredekai anayankha Esitere kuti: “Usaganize kuti iwe wekha udzapulumuka mwa Ayuda onse chifukwa chakuti uli m’nyumba ya mfumu.+ 14 Pakuti ngati iwe ukhala chete pa nthawi ino, thandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina.+ Koma anthu inu, iwe ndi nyumba ya bambo ako, nonse mudzatheratu. Ndipo ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.”+
15 Poyankha, Esitere anatumiza uthenga kwa Moredekai kuti: 16 “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene angapezeke ku Susani+ ndipo musale kudya+ m’malo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ usana ndi usiku. Inenso pamodzi ndi atsikana anga onditumikira+ tisala kudya. Pamenepo, ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu, ndipo ngati n’kufa,+ ndife.” 17 Zitatero Moredekai anapita kukachita zonse zimene Esitere anamuuza.
5 Ndiyeno pa tsiku lachitatu,+ Esitere anavala zovala zachifumu.+ Kenako anakaima m’bwalo lamkati+ la nyumba ya mfumu moyang’anana ndi nyumba ya mfumuyo. Pa nthawiyi mfumu inali itakhala pampando wake wachifumu m’nyumba yakeyo moyang’anana ndi khomo lolowera m’nyumbayo. 2 Mfumu itangoona Mfumukazi Esitere itaima m’bwalo la nyumba ya mfumu, inamukomera mtima+ moti inamuloza ndi ndodo yachifumu ya golide+ imene inali m’manja mwake. Pamenepo Esitere anayandikira ndi kugwira pamwamba pa ndodoyo.
3 Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Chavuta n’chiyani Mfumukazi Esitere, ndipo ukufuna kupempha chiyani?+ Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu,+ ipatsidwa kwa iwe.” 4 Pamenepo Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, lero inu ndi Hamani+ mubwere kuphwando+ limene ine ndakukonzerani.” 5 Ndiyeno mfumu inati: “Amuna inu, itanani Hamani mofulumira+ mogwirizana ndi mawu a Esitere.” Kenako mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Esitere anakonza.
6 Pa nthawi ina mkati mwa phwando la vinyo, mfumu inafunsa Esitere kuti: “Ukufuna kupempha chiyani?+ Chimene ukufunacho ndikupatsa. Ukufuna chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu, ipatsidwa kwa iwe.” 7 Poyankha Esitere anati: “Pempho langa ndi ili, 8 Ngati mungandikomere mtima mfumu+ ndipo ngati zingakukomereni kuchita zimene ndapempha n’kundipatsa zimene ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzerani mawa. Ndipo mawa ndidzanena pempho langa monga mmene inu mfumu mwanenera.”+
9 Pamapeto pake, Hamani anatuluka tsiku limenelo ali wokondwa+ komanso akusangalala kwambiri mumtima mwake. Koma atangoona Moredekai pachipata cha mfumu+ komanso kuti sanaimirire+ ndi kunthunthumira chifukwa cha iye,+ nthawi yomweyo Hamani anamukwiyira kwambiri+ Moredekai. 10 Koma Hamani anaugwira mtima ndipo analowa m’nyumba yake. Kenako anatumiza uthenga kuti anzake ndi mkazi wake Zeresi+ abwere. 11 Ndiyeno Hamani anayamba kudzitamandira pamaso pawo chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chake+ ndi kuchuluka kwa ana ake aamuna.+ Anadzitamandiranso chifukwa cha zonse zimene mfumu inamulemekeza nazo komanso chifukwa chakuti inamukweza kuposa akalonga ndi atumiki a mfumu.+
12 Pamenepo Hamani anapitiriza kunena kuti: “Kuwonjezera apo, Mfumukazi Esitere sanaitane wina aliyense kuphwando limene anakonza, koma anaitana ine ndi mfumu,+ ndipo mawa+ wandiitananso pamodzi ndi mfumu. 13 Koma zonsezi sizikundikwanira ndikamaona Moredekai, Myuda, atakhala pachipata cha mfumu.” 14 Pamenepo mkazi wake Zeresi ndi anzake onsewo anamuuza kuti: “Mukonzetse mtengo+ wotalika mikono* 50. Ndiyeno m’mawa+ mukauze mfumu kuti apachike Moredekai pamtengowo.+ Mukatero mupite kuphwando ndi mfumu muli wosangalala.” Zimenezi zinaoneka zosangalatsa+ kwa Hamani, choncho anakonzetsa mtengowo.+
6 Usiku umenewo mfumu inasowa tulo.+ Choncho inaitanitsa buku limene anali kulembamo zochitika+ za m’masiku amenewo. Ndiyeno anawerenga zochitikazo pamaso pa mfumu. 2 M’bukumo anapeza kuti mwalembedwa zimene Moredekai anaulula+ zokhudza Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri+ za panyumba ya mfumu, alonda apakhomo, amene anafuna kupha Mfumu Ahasiwero. 3 Pamenepo mfumu inati: “Kodi Moredekai walandira ulemu ndi zinthu zazikulu zotani chifukwa cha zimene anachitazi?” Poyankha atumiki a mfumu, nduna zake, zinati: “Palibe chimene walandira.”+
4 Kenako mfumu inati: “Kodi m’bwalo muli ndani?” Tsopano Hamani anali atalowa m’bwalo lakunja+ kwa nyumba ya mfumu kudzauza mfumu kuti apachike Moredekai pamtengo+ umene anamukonzera. 5 Pamenepo atumiki a mfumu anati: “Hamani+ waima m’bwalomo.” Ndiyeno mfumu inati: “Muuzeni alowe.”
6 Hamani atalowa, mfumu inam’funsa kuti: “Kodi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu tim’chitire chiyani?”+ Atamva zimenezi, Hamani ananena mumtima mwake kuti: “Kodi winanso ndani amene mfumu ingafune kum’patsa ulemu kuposa ine?”+ 7 Choncho Hamani anauza mfumu kuti: “Munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu, 8 amubweretsere zovala zachifumu+ zimene mfumu imavala ndi hatchi* imene mfumu imakwera.+ Hatchiyo aiveke duku lachifumu. 9 Ndiyeno chovalacho ndi hatchiyo azipereke kwa mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu.+ Akalongawo aveke chovalacho munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemuyo ndipo amukweze pahatchiyo ndi kumuyendetsa m’bwalo+ la mzinda.+ Ndipo azifuula pamaso pake kuti, ‘Umu ndi mmene timachitira ndi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu.’”+ 10 Nthawi yomweyo mfumu inauza Hamani kuti: “Fulumira, tenga chovala ndi hatchi monga mmene wanenera, ndipo ukachitire zimenezi Moredekai, Myuda, amene ali kuchipata. Uonetsetse kuti zonse zimene wanenazi zakwaniritsidwa.”+
11 Pamenepo Hamani anatenga chovala+ ndi hatchi, ndipo chovalacho anaveka Moredekai.+ Kenako anam’kwezeka pahatchiyo ndi kumuyendetsa m’bwalo+ la mzinda, akufuula pamaso pake kuti:+ “Umu ndi mmene timachitira ndi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu.”+ 12 Zimenezi zitachitika, Moredekai anabwerera kuchipata cha mfumu.+ Koma Hamani anapita kunyumba kwake mofulumira, akulira ndiponso ataphimba kumutu.+ 13 Ndiyeno Hamani anafotokozera Zeresi+ mkazi wake ndi anzake onse chilichonse chimene chinam’chitikira. Pamenepo amuna anzeru+ amene anali kum’tumikira ndi Zeresi mkazi wake anati: “Ngati n’zoona kuti Moredekai amene iwe wayamba kugonja pamaso pake ndi Myuda, sudzamugonjetsa koma udzagonja ndithu pamaso pake.”+
14 Pamene anali kukambirana naye zimenezi, nduna za panyumba ya mfumu zinafika, ndipo mofulumira+ zinatenga Hamani ndi kupita naye kuphwando+ limene Esitere anakonza.
7 Kenako mfumu ndi Hamani+ anafika kudzachita phwando ndi Mfumukazi Esitere. 2 Tsopano mfumu inafunsanso Esitere pa tsiku lachiwiri la phwando la vinyo kuti:+ “Ukufuna kupempha chiyani+ Mfumukazi Esitere? Chimene ukufunacho ndikupatsa.+ Ukufuna chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu,+ ipatsidwa kwa iwe.” 3 Pamenepo Mfumukazi Esitere inayankha kuti: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomereni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga+ komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.+ 4 Pakuti ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa+ kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa.+ Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna+ ndi akapolo aakazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.”
5 Tsopano Mfumu Ahasiwero inalankhula ndipo inafunsa Mfumukazi Esitere kuti: “Ndani wachita zimenezi,+ ndipo ali kuti munthu amene wadzikuza+ ndi kuchita zinthu zoterezi?” 6 Poyankha Esitere anati: “Munthu wake ndi uyu, Hamani, mdani ndiponso munthu woipa.”+
Pamenepo Hamani anachita mantha+ chifukwa cha mfumu ndi mfumukazi. 7 Ndiyeno mfumu inanyamuka mokwiya+ kuchoka paphwando la vinyo ndi kupita kumunda wamaluwa wa panyumba ya mfumu. Pamenepo Hamani ananyamuka kuti apemphe Mfumukazi Esitere kuti ipulumutse moyo wake,+ chifukwa anaona kuti mfumu yatsimikiza zomupatsa chilango.+ 8 Kenako mfumu inabwera kuchokera kumunda wamaluwa wa panyumba ya mfumu ndi kulowanso m’nyumba imene munali phwando la vinyo.+ Pamenepo inaona Hamani atadzigwetsa pampando wokhala ngati bedi+ pamene panali Esitere. Choncho mfumu inati: “Kodi ukufunanso kugwirira mfumukazi ine ndili m’nyumba mom’muno?” Mfumu italankhula,+ Hamani anamuphimba nkhope. 9 Haribona,+ mmodzi mwa nduna za panyumba ya mfumu+ amene anali pamaso pa mfumu anati: “Palinso mtengo+ umene Hamani anapangira Moredekai, amene analankhula zabwino za mfumu.+ Mtengowu uli m’nyumba ya Hamani ndipo ndi wotalika mikono 50.” Pamenepo mfumu inati: “Amuna inu, kam’pachikeni pamtengo umenewo.”+ 10 Choncho anapachika Hamani pamtengo+ umene anakonzera Moredekai,+ ndipo mkwiyo wa mfumu unatha.
8 Tsiku limenelo, Mfumu Ahasiwero inapereka kwa mfumukazi Esitere nyumba ya Hamani,+ amene anali kuchitira nkhanza Ayuda.+ Ndipo Moredekai anabwera pamaso pa mfumu chifukwa Esitere anali atauza mfumu ubale umene unalipo pakati pawo.+ 2 Ndiyeno mfumu inavula mphete yake yodindira+ imene inalanda Hamani ndi kuipereka kwa Moredekai. Pamenepo Esitere anaika Moredekai kuti ayang’anire nyumba ya Hamani.+
3 Kuwonjezera pamenepo, Esitere analankhulanso ndi mfumu ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamapazi a mfumuyo. Iye analira+ ndi kuchonderera kuti mfumu imukomere mtima. Ndiponso kuti isinthe choipa+ cha Hamani Mwagagi ndi chiwembu+ chimene anakonzera Ayuda.+ 4 Ndiyeno mfumu inaloza Esitere ndi ndodo yachifumu ya golide.+ Zitatero, Esitere anadzuka ndi kuima pamaso pa mfumu. 5 Tsopano Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima,+ komanso ngati n’zoyenera kwa inu mfumu ndiponso ngati ndine munthu wabwino kwa inu, palembedwe makalata ofafaniza makalata+ achiwembu amene Hamani, mwana wa Hamedata Mwagagi,+ analemba pofuna kuwononga Ayuda+ amene ali m’zigawo zanu zonse mfumu.+ 6 Ndingapirire bwanji pamene ndikuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndipo ndingapirire bwanji pamene ndikuona abale anga akuwonongedwa?”
7 Choncho Mfumu Ahasiwero inauza mfumukazi Esitere ndi Moredekai Myuda kuti: “Nyumba ya Hamani ndaipereka kwa Esitere,+ ndipo Hamani wapachikidwa pamtengo+ chifukwa chakuti anatambasula dzanja lake ndi kuukira Ayuda. 8 Ndiye inu lembani makalata m’malo mwa Ayuda. Mulembe zimene mukuona kuti n’zabwino kwa inu m’dzina la mfumu.+ Mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu, pakuti n’zosatheka kufafaniza makalata amene alembedwa m’dzina la mfumu ndi kudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+
9 Choncho anaitana alembi+ a mfumu pa nthawi imeneyo, m’mwezi wachitatu umene ndi mwezi wa Sivani,* pa tsiku la 23 la mweziwo. Iwo analemba makalatawo mogwirizana ndi zimene Moredekai ananena. Makalatawo anali opita kwa Ayuda, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi akalonga a m’zigawo zonse kuchokera ku Indiya kukafika ku Itiyopiya, zigawo 127.+ Chigawo chilichonse anachilembera makalata amenewa malinga ndi mmene anthu a m’chigawocho anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo.+ Nawonso Ayuda anawalembera malinga ndi mmene iwo anali kulembera ndiponso m’chinenero chawo.+
10 Moredekai analemba makalatawo m’dzina la Mfumu+ Ahasiwero ndi kuwadinda+ ndi mphete yodindira ya mfumu.+ Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma okwera pamahatchi+ aliwiro amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu. 11 M’makalatawo mfumu inalola Ayuda amene anali m’mizinda yosiyanasiyana kuti asonkhane+ ndi kuteteza miyoyo yawo. Inawalolanso kuwononga, kupha ndi kufafaniza magulu onse ankhondo a anthu+ ndi zigawo zimene zinali kuwachitira nkhanza, ngakhalenso ana ndi akazi ndiponso kufunkha zinthu zawo.+ 12 Mfumu inawalola kuchita zimenezi m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi,+ tsiku la 13+ la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 13 Zimene analemba+ m’makalatawo anazipereka kuti zikhale lamulo m’zigawo zonse. Anazifalitsa kwa anthu a mitundu yonse kuti Ayuda akonzekere kudzabwezera+ adani awo pa tsiku limeneli. 14 Amtokomawo+ anathamanga ndi kupita mofulumira atakwera pamahatchi amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu. Anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndipo lamulo linachokera m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+
15 Ndiyeno Moredekai anachoka pamaso pa mfumu atavala chovala chachifumu+ cha buluu ndi nsalu yoyera. Analinso atavala chisoti chachikulu chachifumu chagolide, mkanjo wa nsalu yabwino kwambiri yaubweya wa nkhosa+ wonyika mu utoto wofiirira.+ Ndipo mumzinda wa Susani munamveka kufuula kwa chisangalalo ndi kukondwera.+ 16 Pakati pa Ayuda panali chisangalalo, kukondwa+ ndi kunyadira ndipo anthu anali kuwapatsa ulemu. 17 M’zigawo zonse ndi m’mizinda yonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake linafika, Ayuda anali kusangalala ndi kukondwera. Anachita phwando+ ndipo linali tsiku lachisangalalo. Anthu ambiri+ a m’dzikomo anayamba kudzitcha Ayuda+ chifukwa anali kuchita mantha kwambiri+ ndi Ayudawo.
9 Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,*+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi chilamulo chake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda anali kuyembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayudawo ndi amene anagonjetsa anthu amene anali kudana nawo.+ 2 Ayuda anasonkhana pamodzi+ m’mizinda yawo m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero+ kuti agwire anthu amene anali kufuna kuwachitira zinthu zoipa.+ Ndipo palibe munthu amene analimba mtima pamaso pawo chifukwa anthu a mitundu yonse anali kuopa+ Ayudawo. 3 Akalonga onse+ a m’zigawozo, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi onse ogwira ntchito+ za mfumu anali kuthandiza Ayudawo chifukwa anali kuopa+ Moredekai. 4 Izi zinali choncho chifukwa Moredekai anali ndi udindo waukulu+ m’nyumba ya mfumu ndipo anatchuka+ m’zigawo zonse chifukwa mphamvu zake zinali kukulirakulira.+
5 Ndiyeno Ayuda anakantha adani awo onse ndipo anawapha ndi kuwawononga ndi lupanga.+ Ayudawo anachita zonse zimene anali kufuna kwa anthu amene anali kudana nawo.+ 6 Kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ Ayudawo anapha ndi kuwononga amuna 500. 7 Iwo anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaizata, 10 ana aamuna 10+ a Hamani+ mwana wa Hamedata amene anali kudana ndi Ayuda.+ Ayuda anapha amuna amenewa koma sanafunkhe+ zinthu zawo.
11 Pa tsiku limenelo mfumu anaiuza chiwerengero cha anthu amene anaphedwa kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.
12 Ndiyeno mfumu inauza Mfumukazi Esitere+ kuti: “Kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani+ Ayuda apha ndi kuwononga amuna 500 pamodzi ndi ana 10 a Hamani. Ndiye kuli bwanji nanga m’zigawo zina zonse+ za mfumu?+ Choncho, ukufuna kupempha chiyani? Chimene ukufunacho ndikupatsa.+ Ukufunanso chiyani china?+ Chimene ukufunacho chichitika.” 13 Pamenepo Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu,+ lolani kuti mawa Ayuda amene ali mu Susani achite mogwirizana ndi zimene lamulo laleroli likunena.+ Lolani kuti ana aamuna 10 a Hamani apachikidwe pamtengo.”+ 14 Choncho mfumu inalamula kuti achite zomwezo.+ Pamenepo lamulo linaperekedwa ku Susani, ndipo ana aamuna 10 a Hamani anapachikidwa.
15 Ndiyeno Ayuda amene anali ku Susani anasonkhananso pamodzi pa tsiku la 14+ la mwezi wa Adara, ndipo anapha amuna 300 ku Susani, koma sanafunkhe zinthu zawo.+
16 Ayuda ena onse amene anali m’zigawo+ za mfumu anasonkhana pamodzi kuti ateteze miyoyo yawo.+ Ndipo anabwezera+ adani awo ndi kupha anthu 75,000 amene anali kudana nawo, koma sanafunkhe zinthu zawo 17 pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Ndiyeno pa tsiku la 14 la mweziwo anapuma ndi kulisandutsa tsiku laphwando+ ndi lachikondwerero.+
18 Ayuda amene anali ku Susani anasonkhana pamodzi pa tsiku la 13+ ndi la 14 la mweziwo. Ndipo pa tsiku la 15 la mweziwo anapuma ndipo analisandutsa tsiku laphwando ndi lachikondwerero.+ 19 N’chifukwa chake Ayuda akumidzi amene anali kukhala m’madera akutali ndi mzinda, anasandutsa tsiku la 14 la mwezi wa Adara+ kukhala tsiku lachikondwerero,+ laphwando, losangalala ndiponso tsiku+ lotumizirana chakudya.+
20 Ndiyeno Moredekai+ analemba zochitika zimenezi ndi kutumiza makalata kwa Ayuda onse amene anali m’zigawo zonse+ za Mfumu Ahasiwero, zakutali ndi zapafupi zomwe. 21 M’makalatawo anawalamula kuti pa tsiku la 14 ndi la 15 la mwezi wa Adara azichita+ chikondwerero chimenechi nthawi zonse chaka ndi chaka. 22 Anawalamula kuti masiku amenewa akhale ochita phwando, kusangalala, kutumizirana chakudya+ ndi kupereka mphatso kwa anthu osauka.+ Anatero pakuti amenewa ndi masiku amene Ayuda anasiya kuvutitsidwa ndi adani awo,+ komanso mwezi umene chisoni chawo chinasintha kukhala chikondwerero ndiponso pamene tsiku lolira+ linasintha kukhala tsiku losangalala.
23 Ndipo Ayuda anavomereza kuti masiku amenewa akhale achikondwerero chimene anali atayamba kale kuchita. Anavomereza zimenezo mogwirizananso ndi zimene Moredekai anawalembera. 24 Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata+ Mwagagi,+ amene anali kudana+ ndi Ayuda onse, anakonzera Ayudawo chiwembu kuti awawononge.+ Choncho iye anachita Puri+ kapena kuti Maere,+ ndi cholinga chakuti awasautse ndi kuwawononga. 25 Koma Esitere ataonekera pamaso pa mfumu, mfumuyo inalemba lamulo lakuti:+ “Chiwembu+ chake choipa chimene anakonzera Ayuda chimugwere iyeyo.”+ Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+ 26 N’chifukwa chake masiku amenewa anawatcha kuti Purimu, kutengera dzina la Puri.+ Choncho mogwirizana ndi mawu onse a m’kalata imeneyi+ komanso chifukwa cha zimene anaona pa nkhani imeneyi ndi zimene zinawachitikira, 27 Ayudawo anaika lamulo ndi kuvomereza kuti iwo, ana awo ndi anthu onse odziphatika kwa iwo+ adzatsatira lamuloli. Lamuloli linali lakuti, nthawi zonse azisunga masiku awiri amenewa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa zokhudza masikuwa komanso kuti aziwasunga pa nthawi yoikidwiratu chaka ndi chaka. 28 Anayenera kukumbukira masiku amenewa mu m’badwo uliwonse, banja lililonse, chigawo chilichonse ndi mzinda uliwonse. Ayuda sanayenere kusiya kusunga masiku a Purimu ndipo ana awo sanayenere kusiya kukumbukira masiku amenewa.+
29 Ndiyeno Mfumukazi Esitere, mwana wamkazi wa Abihaili,+ pamodzi ndi Moredekai Myuda, analemba kalata yachiwiri ndi ulamuliro wonse, kutsimikizira za Purimu. 30 Kenako anatumiza makalata a mawu amtendere ndi odalirika+ kwa Ayuda onse m’zigawo 127+ zimene Ahasiwero+ anali kulamulira. 31 Anatumiza makalatawo kuti atsimikizire kuti pa nthawi yoikidwiratu, Ayuda onse ndi ana awo azichita chikondwerero cha Purimu monga mmene Moredekai Myuda ndi Mfumukazi Esitere anawalamulira.+ Anawakumbutsanso lamulo limene iwo ndi ana awo+ anadziikira kuti adzasala kudya+ komanso kuti adzapemphera kwa Mulungu.+ 32 Choncho zimene Esitere ananena zinatsimikizira nkhani imeneyi ya Purimu+ ndipo zinalembedwa m’buku.
10 Ndiyeno Mfumu Ahasiwero inayambitsa ntchito ya ukapolo+ m’dzikomo ndi pazilumba+ za m’nyanja.
2 Koma ntchito zonse zamphamvu zimene anachita ndi mawu ofotokoza mphamvu zimene Moredekai+ anali nazo zimene mfumu inam’patsa,+ zinalembedwa m’Buku la zochitika+ za m’masiku a mafumu a Mediya ndi Perisiya.+ 3 Moredekai Myuda anali wachiwiri+ kwa Mfumu Ahasiwero ndipo anali wotchuka pakati pa Ayuda. Khamu lonse la abale ake linali kukondwera naye. Iye anali kuchitira zabwino anthu a mtundu wake ndi kulankhula zamtendere+ kwa ana awo onse.
“Ahaswero” amatchedwa Aritasasita m’Baibulo la Septuagint. Anthu amati iyeyu anali Sasita Woyamba, mwana wamwamuna wa Dariyo Wamkulu (Dariyo Hisitasipi).
“Pofeli” ndi mtundu wa mwala wolimba kwambiri. Kawirikawiri mwala umenewu umaoneka wakuda mofiirira, wokhala ndi mawanga oyera ndipo ndi wamtengo wapatali kwambiri.
“Mule” ndi madzi onunkhira ochokera kumitengo inayake, ndipo nthawi zina madziwa anali kupangira mafuta odzola.
Onani Zakumapeto 13.
Onani Zakumapeto 13.
Mawu akuti “Puri” amatanthauza “Maere.” Apa ndi pamene panachokera dzina la mwambo wachiyuda wa “Purimu,” wochitika m’mwezi wa 12 pakalendala yopatulika. Onani Zakumapeto 13.
Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Ena amati “saka.”
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Onani Zakumapeto 13.
Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.