Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Job 1:1-42:17
  • Yobu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yobu
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yobu

Yobu

1 Kudziko la Uzi+ kunali munthu wina dzina lake Yobu.+ Iye anali munthu wopanda cholakwa,+ wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+ 2 Yobu anali ndi ana aamuna 7, ndi ana aakazi atatu.+ 3 Iye anali ndi ziweto+ izi: Nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ng’ombe 1,000 zomwe zinali kugwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 500. Analinso ndi antchito ochuluka zedi, ndipo iye anali munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.+

4 Ana ake aamuna anali kuchita phwando+ kunyumba ya aliyense wa iwo, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina, ndipo anali kuitana alongo awo atatu kuti adzadye ndi kumwera limodzi. 5 Akamaliza kuchita maphwando kunyumba zawo zonse, Yobu anali kutumiza uthenga n’kuwauza kuti adziyeretse.+ Kenako iye anali kudzuka m’mawa kwambiri n’kupereka nsembe zopsereza+ mogwirizana ndi chiwerengero cha ana ake onse, popeza iye ankati, “mwina ana anga achimwa ndipo anyoza+ Mulungu mumtima mwawo.”+ Umu ndi mmene Yobu anali kuchitira nthawi zonse.+

6 Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona+ ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo ngakhalenso Satana+ anapita nawo limodzi.+

7 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi+ ndi kuyendayendamo.”+ 8 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu, poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi?+ Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa+ ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndi wopewa zoipa.”+ 9 Pamenepo Satana anamuyankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?+ 10 Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo?+ Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi. 11 Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+ 12 Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako. Koma iyeyo usam’tambasulire dzanja lako ndi kum’khudza.” Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova.+

13 Tsopano linafika tsiku limene ana a Yobu, aamuna ndi aakazi, anali kudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya m’bale* wawo woyamba kubadwa.+ 14 Kenako kunabwera munthu+ kwa Yobu kudzanena uthenga wakuti: “Ng’ombe zinali kulima+ ndipo abulu aakazi anali kudya msipu chapambali pake. 15 Ndiyeno kunabwera Asabeya+ omwe alanda ziwetozo n’kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”+

16 Uyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Moto wa Mulungu watsika kuchokera kumwamba,+ ndipo wayaka pakati pa nkhosa ndi abusa n’kupsereza nkhosazo ndi abusawo. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

17 Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Kunabwera magulu atatu a Akasidi+ omwe anafika mwaliwiro kwambiri, n’kulanda ngamila ndi kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

18 Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu winanso kudzanena kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi anali kudya ndi kumwa vinyo+ m’nyumba ya m’bale wawo woyamba kubadwa. 19 Kenako kunabwera chimphepo+ kuchokera kudera la kuchipululu chomwe chinawomba makona anayi a nyumbayo, ndipo nyumbayo yagwera anawo n’kuwapha. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

20 Yobu atamva zimenezi anaimirira n’kung’amba+ malaya ake akunja odula manja. Anametanso tsitsi+ kumutu kwake, kenako anagwada pansi+ n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ 21 n’kuyamba kunena kuti:

“Ndinatuluka m’mimba mwa mayi anga ndili wamaliseche,+

Ndipo ndidzabwerera mmenemo ndilinso wamaliseche.+

Yehova wapereka,+ ndipo Yehova yemweyo watenga.+

Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”+

22 M’zonsezi Yobu sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.+

2 Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova, ndipo nayenso Satana anapita nawo limodzi kukaonekera pamaso pa Yehova.+

2 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi ndi kuyendayendamo.”+ 3 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu,+ poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi? Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+ Komabe iye akadali ndi mtima wosagawanika+ ngakhale kuti iweyo ukundiumiriza+ kuti ndimuwononge popanda chifukwa.”+ 4 Koma Satana+ anamuyankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.+ 5 Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+

6 Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, ndam’pereka m’manja mwako. Koma samala kuti usakhudze moyo wake.” 7 Kenako Satana anachoka pamaso pa Yehova+ n’kukagwetsera Yobu zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu. 8 Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikanda nalo ndipo anali kukhala paphulusa.+

9 Patapita nthawi, mkazi wake anam’funsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala ndi mtima wosagawanika?+ Tukwanani Mulungu mufe!” 10 Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa.+ Kodi tizingolandira zabwino zokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ M’zonsezi Yobu sanachimwe ndi milomo yake.+

11 Tsopano anzake atatu a Yobu anamva za tsoka lonse limene linamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi wa ku Temani,+ Bilidadi wa ku Shuwa+ ndi Zofari wa ku Naama.+ Iwo anakumana pamodzi atachita kupangana+ kuti apite kukazonda Yobu ndi kukamulimbikitsa.+ 12 Atakweza maso awo ali chapatali, sanamuzindikire poyamba. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo aliyense anang’amba+ malaya ake akunja odula manja, n’kuwaza fumbi m’mwamba pamwamba pa mitu yawo.+ 13 Kenako anakhala+ naye limodzi pansi masiku 7 usana ndi usiku, ndipo palibe amene anali kumulankhula chilichonse popeza iwo anaona kuti ululu+ wake unali waukulu kwambiri.

3 Pambuyo pa zimenezi m’pamene Yobu anatsegula pakamwa pake n’kuyamba kutemberera tsiku limene anabadwa.+ 2 Tsopano Yobu anati:

 3 “Liwonongeke tsiku limene ndinabadwa,+

Ndiponso usiku umene wina ananena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu wapangika m’mimba.’

 4 Tsiku limenelo likhale mdima.

Mulungu asaliganizirenso ali kumwamba,

Ndipo kuwala kusalifikire.

 5 Mdima wandiweyani ulitenge.

Mtambo wa mvula uliphimbe.

Zinthu zimene zimadetsa tsiku ziliopseze.+

 6 Usiku umenewo utengedwe ndi mdima.+

Usasangalale pakati pa masiku a pachaka,

Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.

 7 Ndithu usiku umenewo ukhale wosabereka.

Mfuu yachisangalalo isamveke usikuwo.+

 8 Otemberera masiku alitemberere tsikulo,

Iwo amene ali okonzeka kudzutsa ng’ona.*+

 9 Nyenyezi za m’chisisira cha m’mawa mwake zizime.

Lidikire kuwala koma lisakuone,

Ndipo lisaone kuwala kwa m’bandakucha.

10 Chifukwa silinatseke zitseko za mimba ya mayi anga,+

Kuti ndisaone mavuto.

11 Bwanji sindinafere m’chiberekero?+

Bwanji sindinamwalire nditangotuluka m’mimba?

12 N’chifukwa chiyani mawondo anakumana nane,

Ndipo mabere+ ndinakumana nawo chifukwa chiyani kuti ndiyamwe?

13 Panopa bwenzi nditagona kuti ndisasokonezedwe,+

Bwenzi ndili m’tulo pa nthawiyo, ndipo bwenzi pano ndikupuma+

14 Limodzi ndi mafumu ndi aphungu a padziko lapansi,+

Amene anadzimangira malo omwe tsopano ali bwinja.+

15 Kapena ndi akalonga amene ali ndi golide,

Amene amadzaza nyumba zawo ndi siliva.

16 Kapena ngati pakati pomwe papita pachabe mosadziwa,+ bwenzi ine kulibe,

Mofanana ndi ana amene sanaone kuwala.+

17 Kumandako oipa asiya kusautsika,+

Ndipo kumeneko anthu omwe mphamvu zawo zatha, akupuma.+

18 Akaidi onse pamodzi ali pa mtendere.

Iwo samvanso mawu a munthu wowakusira ku ntchito.+

19 Aang’ono ndi aakulu amakhala chimodzimodzi kumeneko,+

Ndipo kapolo amamasuka kwa mbuye wake.

20 N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene ali ndi mavuto,

Ndiponso moyo kwa opwetekedwa mtima?+

21 N’chifukwa chiyani anthu ena amadikirira imfa, koma siwabwerera,+

Ngakhale amakumba pansi poifunafuna, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika?

22 Amenewa amasangalala kwadzaoneni,

Amakondwera akapeza manda.

23 N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa mwamuna wamphamvu amene njira yake yabisika,+

Amene Mulungu akum’pingapinga?+

24 Pakuti chakudya changa chimabwera limodzi ndi kuusa moyo,*+

Ndipo ngati madzi, kubuula kwanga kumakhuthuka.+

25 Chinthu chochititsa mantha chimene ndinali kuchita nacho mantha, chandibwerera,

Ndipo chimene ndinali kuchiopa chabwera kwa ine.+

26 Sindinali wopanda nkhawa kapena wopanda mavuto,

Komanso sindinali pa mtendere, komabe zosautsa mtima zandibwerera.”

4 Tsopano Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:

 2 “Munthu akayesa kukulankhula, kodi utopa?

Koma ndani angathe kudziletsa kuti asalankhule?

 3 Iweyo walangiza anthu ambiri,+

Ndipo manja ofooka unali kuwalimbitsa.+

 4 Aliyense wofuna kugwa, mawu ako anali kumudzutsa,+

Ndipo mawondo olobodoka unali kuwachirikiza.+

 5 Koma panopa zili pa iwe, ndipo watopa nazo,

Zakhudza iwe, ndipo wasokonezeka nazo.

 6 Popeza umaopa Mulungu, kodi sukuyenera kulimba mtima?

Kodi ulibe chiyembekezo, munthu woti ukuyenda ndi mtima wosagawanika?+

 7 Takumbukira: Kodi ndani wosalakwa amene anawonongedwapo?

Ndipo n’kuti kumene anthu owongoka mtima+ anafafanizidwapo?

 8 Malinga ndi zimene ine ndaona, anthu okonzera anzawo zopweteka,

Ndi ofesa mavuto, amakolola zomwezo.+

 9 Iwo amawonongeka ndi mpweya wa Mulungu,

Ndipo ndi mphamvu ya mkwiyo wake, amatha.

10 Mkango umabangula, ndipo mkango wamphamvu umamveka kulira,

Koma ngakhale mano a mkango wamphamvu, amathyoka.

11 Mkango umafa posowa nyama yoti udye,

Ndipo ana a mkango amalekanitsidwa.

12 Tsopano mawu anabwera kwa ine mwakachetechete,

Ndipo khutu langa linamva kunong’ona kwa mawuwo.+

13 Ndinakhala ndi malingaliro osautsa chifukwa cha masomphenya amene ndinaona usiku,

Pa nthawi imene anthu amakhala ali m’tulo tofa nato.

14 Ndinachita mantha kwambiri ndiponso ndinanjenjemera,

Ndipo mafupa anga onse anadzaza mantha.

15 Mzimu unadutsa kumaso kwanga,

Ndipo ubweya wa pathupi langa unayamba kuimirira.

16 Mzimuwo unaima chilili,

Koma sindinazindikire maonekedwe ake.

Chinthu chinaima pamaso panga.

Kunali bata, kenako ndinamva mawu akuti:

17 ‘Kodi munthu angakhale wolungama kuposa Mulungu?

Kapena kodi munthu angakhale woyera kuposa amene anam’panga?’

18 Iyetu sakhulupirira atumiki ake,

Ndipo angelo* ake amawapezera zifukwa.

19 Nanga kuli bwanji anthu okhala m’nyumba zadothi,

Amene maziko awo ali m’fumbi?+

Iwo amathudzulidwa mosavuta kuposa kadziwotche.

20 Kuyambira m’mawa mpaka madzulo, amakhala akunyenyedwa.

Amawonongeka kwamuyaya, popanda aliyense kukhudzika nazo.

21 Kodi chingwe cha hema wawo chimene chili mkati mwawo, sichinasololedwe?

Iwo amafa chifukwa chosowa nzeru.

5 “Taitana! Kodi pali aliyense amene akukuyankha?

Ndipo kodi utembenukira kwa mngelo* uti?

 2 Chifukwa wopusa, mkwiyo udzamupha,

Ndipo nsanje ya munthu wosachedwa kukopeka idzamupha.

 3 Ineyo ndaonapo wopusa akuzika mizu,+

Koma mwadzidzidzi ndinayamba kutemberera malo ake okhala.

 4 Ana ake amakhala kutali ndi chipulumutso,+

Ndipo amaponderezedwa pachipata, popanda wowapulumutsa.

 5 Zimene iye amakolola, munthu wanjala amazidya.

Ngakhale nyama yake imene waipha n’kuikoloweka pangowe, wina amadzaitenga,

Ndipo msampha umawalanda zofunika pa moyo wawo.

 6 Pajatu zopweteka sizichokera m’fumbi,

Ndipo mavuto satuluka m’nthaka.

 7 Pakuti munthu amabadwa kuti akumane ndi mavuto,

Monga momwe mbaliwali zimathethekera m’mwamba kuchokera pamoto.

 8 Koma ndikanakhala ine, ndikanafunsa kwa Mulungu,

Ndipo kwa Mulunguyo, ndikanatula mlandu wanga.+

 9 Kwa Iye amene amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,

Zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+

10 Kwa Iye amene amapereka mvula padziko lapansi,+

Ndi kupititsa madzi pabwalo.+

11 Kwa Iye amene amaika anthu onyozeka pamalo okwezeka,+

Mwakuti anthu achisoni amakhala pamwamba, pomwe amapezapo chipulumutso.

12 Kwa Iye amene amalepheretsa zolinga za ochenjera,+

Mwakuti ntchito imene manja awo amagwira siioneka.

13 Kwa Iye amene amakola anzeru m’kuchenjera kwawo,+

Iye amene amachititsa kuti malangizo a ochenjera abweretse chisokonezo.+

14 Iwo amakumana ndi mdima ngakhale masana,

Ndipo amafufuzafufuza masanasana ngati kuti ndi usiku.+

15 Kwa Iye amene amapulumutsa munthu ku lupanga lochokera m’kamwa mwa oipa,

Ndi kupulumutsa wosauka m’manja mwa wamphamvu.+

16 Mwakuti wonyozeka amapeza chiyembekezo,+

Koma anthu opanda chilungamo amatseka pakamwa pawo.+

17 Tamvera! N’ngodala munthu amene Mulungu amam’dzudzula,+

Ndipo chilango* cha Wamphamvuyonse usachikane.

18 Pakuti iye amayambitsa kupweteka, koma amamanga chilonda chopwetekacho.

Amaphwanya anthu, koma manja ake ndi amene amawachiritsa.

19 Adzakulanditsa m’masautso 6,+

Ndipo m’masautso 7, palibe choipa chimene chidzakukhudze.+

20 Pa nthawi yanjala, adzakulanditsa ndithu ku imfa,+

Ndipo pa nkhondo adzakupulumutsa ku mphamvu ya lupanga.

21 Udzabisidwa ku lilime lomenya ngati chikwapu,+

Ndipo sudzachita mantha ikadzafika nthawi yowononga.

22 Pa nthawi yowononga ndi yanjala, iweyo udzaseka,

Ndipo nyama zakutchire sudzaziopa.

23 Udzachita pangano ndi miyala yakutchire,

Ndipo nyama zakutchire zidzakhala nawe pa mtendere.+

24 Udzaona ndithu kuti mtendere ndiwo hema wako,

Ndipo ukapita kukayendera malo ako odyetserako ziweto, udzaona kuti palibe chimene chikusowa.

25 Ndithu udzaona kuti ana ako ndi ambiri,+

Ndipo mbadwa zako zidzakhala ngati zomera za padziko lapansi.+

26 Udzakhala ndi mphamvube mpaka kulowa m’manda,+

Mofanana ndi ngala zokhwima za tirigu, zimene amazisanjikiza pamodzi pamalo opunthira tirigu pa nyengo yake.

27 Izi n’zimene tafufuza ndipo zilidi choncho.

Imva zimenezi ndi kuzitsatira.”

6 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Zikanakhala bwino masautso anga+ onse akanayezedwa kulemera kwake,

Ndiponso pa nthawi yomweyo mavuto anga akanaikidwa pasikelo.

 3 Chifukwa panopa akulemera kuposa mchenga wam’nyanja.

N’chifukwa chake ndalankhula zopanda pake.+

 4 Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilasa,+

Ndipo ine ndikumwa poizoni wa miviyo.+

Zoopsa zochokera kwa Mulungu zasonkhana kuti zilimbane nane.+

 5 Kodi mbidzi+ imalira ikudya msipu?

Kapena ng’ombe yamphongo imalira ikudya chakudya chake?

 6 Kodi chakudya chosakoma chingadyedwe chopanda mchere?

Kapena kodi utomoni* wa zomera umakoma?

 7 Moyo wanga wakana kukhudza zinthu zoterozo.

Zili ngati matenda m’chakudya changa.

 8 Zikanakhala bwino pempho langa likanayankhidwa,

Ndiponso Mulungu akanandipatsa chiyembekezo.

 9 Zikanakhala bwino Mulungu akanati angondiphwanya,

Akanati atambasule dzanja lake n’kundipha.+

10 Ngakhale zimenezo, bwenzi zili zonditonthoza.

Ndikadadumpha ndi chisangalalo+ ngakhale kuti ndikumva ululu wosalekeza,

Chifukwa sindinabise mawu+ a Woyerayo,+ ngakhale kuti iye sakanandichitira chisoni.

11 Kodi ndili ndi mphamvu zochuluka motani, kuti ndizidikirabe?+

Ndipo kodi mapeto anga ndi otani, kuti ndipitirize kutalikitsa moyo wanga?

12 Kodi mphamvu zanga ndi mphamvu za miyala?

Kapena kodi mnofu wanga ndi wamkuwa?

13 Ndilibenso mphamvu zodzithandizira,

Ndipo sindingathenso kugwira ntchito bwinobwino.

14 Aliyense wosasonyeza mnzake kukoma mtima kosatha,+

Adzasiyanso kuopa Wamphamvuyonse.+

15 Ngakhale abale anga amene, achita zachinyengo+ ngati mtsinje woyenda nthawi yozizira,

Ngati makwawa a mitsinje yoyenda nthawi yozizira, imene imauma.

16 Mitsinjeyo imakhala ndi madzi akuda chifukwa cha kusungunuka kwa madzi oundana,

Ndipo chipale chofewa nachonso chimasungunukira momwemo.

17 Pa nyengo yake imakhala yopanda madzi,+ imakhala chete.

Kukatentha, imauma.+

18 Njira zawo zimakhala zokhotakhota.

Mitsinjeyo imapita kumalo opanda kanthu, n’kutha.

19 Magulu a amtengatenga a ku Tema+ amaifunafuna,

Asabeya+ apaulendo amaidikirira.

20 Amachita manyazi chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro,

Amafika pamalowo n’kukhumudwa.+

21 Mofanana ndi zimenezi, amuna inu mwakhala opanda pake,+

Mwaona zoopsa n’kuyamba kuchita mantha.+

22 Kodi ndinanena kuti, ‘Mundipatse kanthu,

Kapena mutapeko pa chuma chanu n’kundiperekera mphatso?

23 Kapena mundipulumutse m’manja mwa mdani,+

Ndi kundiwombola m’manja mwa anthu ankhanza?’+

24 Mundilangize, ndipo ine ndikhala chete.+

Zimene ndalakwitsa, mundidziwitse.+

25 Mawu olungama, ndithu sapweteka.+

Koma kodi kudzudzula kwanu kuli ndi phindu lanji?+

26 Kodi mwapangana kuti mudzudzule mawu anga,

Chonsecho mawu a munthu wopanda chiyembekezo+ amatengedwa ndi mphepo?+

27 Inutu mukhoza kuchita maere kuti mutenge mwana wamasiye,+

Ndipo mnzanu mukhoza kumugulitsa.+

28 Tsopano tandimvetserani,

Ndipo muone ngati ndilimbe mtima kukunamizani.+

29 Chonde sinthani maganizo anu, kuti pachitike chilungamo.

Ndithu sinthani maganizo. Inetu ndikadali wolungama.+

30 Kodi palilime panga pali zosalungama?

Kapena kodi m’kamwa mwanga simuzindikira mavuto?

7 “Kodi si paja munthu amagwira ntchito yokakamiza+ padziko lapansi?

Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+

 2 Monga kapolo, iye amakhala wefuwefu kufunafuna mthunzi,+

Ndipo ngati munthu waganyu, amadikirira malipiro ake.+

 3 Chotero ndalandira miyezi yachabechabe ngati cholowa,+

Ndipo kuvutika usiku uliwonse+ ndiwo malipiro anga.

 4 Ndikagona ndimanena kuti, ‘Kodi ndidzuka nthawi yanji?’+

Kukada ndimangokhalira kutembenukatembenuka mpaka m’mawa kuli mbuu.

 5 Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi+ ndipo wamatirira fumbi,+

Khungu langa lang’ambika n’kumatuluka mafinya.+

 6 Masiku anga akufulumira+ kuposa mmene chimathamangira chowombera nsalu,

Iwo afika pamapeto popanda chiyembekezo.+

 7 Kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mphepo,+

Ndiponso kuti diso langa silidzaonanso zabwino.

 8 Diso la iye amene amandiona silidzandionanso,

Maso anu adzandiyang’ana, koma ine kudzakhala kulibe.+

 9 Mtambo umafika kumapeto ake n’kutha.

Chimodzimodzi ndi munthu amene wapita ku Manda,* sadzabwerako.+

10 Sadzabwereranso kunyumba yake,

Ndipo anthu a pamalo ake sadzamuzindikiranso.+

11 Choncho, ine sinditseka pakamwa panga.

Ndilankhula chifukwa cha kuvutika mumtima,+

Ndilankhula za nkhawa zanga, chifukwa moyo wanga ukupweteka.

12 Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cha m’nyanja,

Kuti mundiikire mlonda?+

13 Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza,

Bedi langa lindithandiza kusenza nkhawa zanga,’

14 Inuyo mumandiopseza ndi maloto,

Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya.

15 Chotero moyo wanga wasankha kubanika,

Wasankha imfa+ m’malo mwa mafupa angawa.

16 Moyo ndaukana,+ sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.*

Ndisiyeni chifukwa masiku anga ndi ochepa kwambiri.+

17 Kodi munthu ndani+ kuti mumulere,

Ndi kuti muzimuganizira?

18 Iye ndani kuti muzimuganizira m’mawa uliwonse,

Ndi kuti muzimuyesa nthawi zonse?+

19 N’chifukwa chiyani simukusiya kundiyang’ana,+

Kapena kundisiya kuti ndimezeko malovu?

20 Ngati ndachimwa, ndingakuchiteni chiyani Inu amene mumaonetsetsa anthu?+

N’chifukwa chiyani mwalunjika ine, kuti ndikhale cholemetsa kwa inu?

21 N’chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga,+

Ndi kunyalanyaza zolakwa zanga?

Pakuti tsopano ndigona m’fumbi.+

Mudzandifunafuna koma ine kudzakhala kulibe.”

8 Kenako Bilidadi wa ku Shuwa+ anati:

 2 “Kodi ukhala ukulankhula zimenezi mpaka liti,+

Pamene zolankhula za m’kamwa mwako zili ngati mphepo yamphamvu?+

 3 Kodi Mulungu angapotoze chiweruzo?+

Ndipo kodi Wamphamvuyonse angapotoze chilungamo?+

 4 Ngati ana ako amuchimwira,

Mwakuti iye wawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,

 5 Iweyo ukafunafuna Mulungu,+

Ndi kuchonderera Wamphamvuyonse,

 6 Ngati uli woyera ndi wowongoka mtima,+

Bwenzi panopa atadzuka kuti akumvere,

Ndipo ndithu akanabwezeretsa malo ako olungama pamene unali kukhala.

 7 Komanso chiyambi chako chikanaoneka ngati chaching’ono,

Koma mapeto ako akanakhala aakulu kwambiri.+

 8 Tafunsa m’badwo wakale,+

Ndipo ganizira zinthu zimene makolo awo anafufuza.+

 9 Pakuti ife tabadwa dzulo,+ ndipo sitikudziwa kalikonse,

Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi.+

10 Kodi iwo sadzakulangiza, sadzakuuza?

Ndipo kodi iwo sadzalankhula kuchokera mumtima mwawo?

11 Kodi gumbwa*+ amamera n’kutalika pamalo pamene si padambo?

Ndipo kodi bango limakula popanda madzi?

12 Pamene ilo likadali ndi maluwa, lisanazulidwe,

Lingaume msanga udzu wina wonse usanaume.+

13 Ndi mmene zilili njira za onse oiwala Mulungu,+

Ndipo chiyembekezo cha wampatuko chidzatha.+

14 Iye amene chidaliro chake chimatha,

Amene amadalira ulusi* wa kangaude.+

15 Iye adzatsamira nyumba yake, koma siidzakhala chiimire.

Adzaigwira, koma siidzakhalitsa.

16 Iye ali ngati chomera chachiwisi bwino chomwe chikuwombedwa dzuwa.

M’munda mwake, nthambi zake zimakula.+

17 Mizu yake imapiringizanapiringizana pamulu wa miyala.

Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake.

18 Wina akam’meza pamalo ake,+

Malowo adzamukana kuti, ‘Sindinakuonepo.’+

19 Umu ndi mmene moyo wake umathera,+

Ndipo m’fumbimo mumamera zina.

20 Mulungutu sangakane munthu wopanda cholakwa,

Ndipo sangagwire dzanja la ochita zoipa.

21 Adzadzaza m’kamwa mwako ndi kuseka,

Ndipo milomo yako adzaidzaza ndi mfuu yachisangalalo.

22 Anthu odana nawe adzadzazidwa ndi manyazi,+

Ndipo hema wa oipa kudzakhala kulibe.”

9 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.

Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+

 3 Ngati Mulunguyo akufuna kutsutsana naye,+

Munthuyo sangamuyankhe n’kamodzi komwe pamafunso 1,000.

 4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+

Ndani angachite naye makani,* koma osavulala?+

 5 Iye amasuntha mapiri,+ anthu osadziwa n’komwe.

Amawachotsa chifukwa cha mkwiyo.+

 6 Amachititsa dziko lapansi kunjenjemera pamalo ake,

Mwakuti zipilala+ zake zimagwedezeka.

 7 Amauza dzuwa kuti lisawale,

Ndipo amaphimba nyenyezi.+

 8 Kumwamba anakutambasula yekha,+

Ndipo amayenda pamafunde aatali a m’nyanja.+

 9 Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, gulu la nyenyezi la Kesili,

Gulu la nyenyezi la Kima+ ndi zipinda zamkati za Kum’mwera.

10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+

Ndiponso zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+

11 Iyetu amadutsa pafupi nane koma ine osamuona,

Amandipitirira koma ine osamuzindikira.+

12 Ndithu iye amalanda. Ndani angamuletse?

Ndani angamufunse kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+

13 Mulungu sadzabweza mkwiyo wake.+

Anthu othandiza munthu wachiwawa+ amagwa pansi pa mapazi ake.

14 N’chifukwa chake ndikamamuyankha,

Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.+

15 Choncho, sindingamuyankhe ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona.+

Ndingachonderere amene akutsutsana nane pa mlandu.+

16 Nditamuitana, kodi angandiyankhe?+

Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere.

17 Iye amene wandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho,

Wachulukitsa zilonda zanga popanda chifukwa.+

18 Sadzalola kuti ndipumeko mpweya wabwino,+

Chifukwa akungondikhuthulira zinthu zowawa.

19 Ngati kuli wamphamvu kwambiri, ndi iyeyo.+

Ngati pali wolimbikitsa chilungamo, ndikufuna andiitane.

20 Ndikanakhala kuti ndikulondola, pakamwa panga pomwe pakanandinena kuti ndine wolakwa.

Ndikanakhala wosalakwa, iye akanandinena kuti ndine wachinyengo.

21 Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, sindikanadziwa zimenezo,

Ndipo ndikanakana moyo wanga.

22 N’chifukwa chake ndikunena kuti zonsezo mfundo yake ndi imodzi, yakuti:

‘Iye amapha osalakwa komanso oipa.’+

23 Anthu atati afe mwadzidzidzi chifukwa cha kusefukira kwa madzi,

Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.

24 Dziko lapansi laperekedwa m’manja mwa woipa.+

Iye amaphimba nkhope za oweruza ake.

Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?

25 Komanso masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+

Iwo athawa ndipo ndithu sadzaona zabwino.

26 Ayenda ngati ngalawa za bango,

Ngati chiwombankhanga chimene chimauluka uku ndi uko pofunafuna chakudya.+

27 Ngati ndanena kuti, ‘Ndiiwale nkhawa zanga,+

Ndisinthe maonekedwe anga+ ndi kusangalala,’

28 Ndachita mantha ndi zopweteka zanga zonse.+

Ndikudziwa kuti mundiona kuti ndine wolakwa.

29 Ndithu ndidzapezeka kuti ndine wolakwa.

N’chifukwa chiyani ndikuvutika pachabe?+

30 Nditati ndisambe madzi a chipale chofewa,

Ndi kusamba m’manja ndi sopo,+

31 Inuyo mungandiviike m’dzenje,

Ndipo zovala zanga zinganyansidwe nane ndithu.

32 Pakuti iye si munthu+ ngati ine kuti ndimuyankhe,

Kapena kuti tizengane mlandu.

33 Palibe munthu woti agamule mlandu wathu,+

Woti akhale woweruza wathu.

34 Iye achotse ndodo yake pa ine,+

Ndipo kuopsa kwake kusandichititse mantha.

35 Ndilankhule ndipo ndisachite naye mantha,

Chifukwa ine sindiopa kulankhula naye.

10 “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.+

Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga.

Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.

 2 Ndimuuza Mulungu kuti, ‘Musanene kuti ndine woipa.

Ndiuzeni chifukwa chimene mukulimbanirana nane.

 3 Kodi ndi bwino kuti inuyo muchite zoipa,+

Kuti mukane chinthu chimene manja anu anagwira ntchito mwamphamvu pochipanga,+

Ndiponso kuti muvomereze malangizo a anthu oipa?

 4 Kodi maso anu+ ali ngati a munthu,

Kapena kodi mumaona ngati mmene munthu amaonera?+

 5 Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,+

Kapena kodi zaka zanu zili ngati masiku a mwamuna wamphamvu,

 6 Kuti muyese kupeza cholakwa changa,

Ndi kuti muzifunafuna tchimo langa?+

 7 Chonsecho mukudziwa kuti ndine wosalakwa,+

Ndipo palibe wondipulumutsa m’manja mwanu.+

 8 Manja anu omwe ndi amene anandiumba, ndipo anandipanga+

Kuzungulira thupi langa lonse, koma tsopano mukufuna kundimeza.

 9 Chonde kumbukirani kuti munandiumba ndi dongo,+

Ndipo mudzandibwezera kufumbi.+

10 Kodi simunandikhuthule ngati mkaka

Ndi kundisefa ngati mkaka wosasa?+

11 Munandiveka khungu ndiponso mnofu,

Ndipo munandiluka ndi mafupa ndi mitsempha.+

12 Mwandipatsa moyo ndi kundisonyeza kukoma mtima kosatha,+

Ndipo mwa kundisamalira+ mumateteza moyo wanga.

13 Zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu.

Ndikudziwa bwino kuti zinthu zimenezi zili ndi inu.

14 Ngati ndachimwa ndipo inu mwaona zonsezo,+

Ndiponso simunandikhululukire zolakwa zanga,+

15 Ngati ndine wolakwa, tsoka kwa ine!+

Ngati ndine wosalakwa, ndisadzutse mutu wanga.+

Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.+

16 Mutu wanga ukadzikweza,+ mudzandisaka ngati kuti ndinu mkango wamphamvu,+

Ndipo mudzandichitira chinthu chinanso chodabwitsa.

17 Mudzabweretsa mboni zanu zatsopano pamaso panga,

Ndipo mudzakulitsa mkwiyo wanu pa ine.

Mavuto anga akungotsatizanatsatizana.

18 Kodi munanditulutsiranji m’mimba?+

Zikanakhala bwino ndikanafa kuti diso ndi limodzi lomwe lisandione.

19 Bwenzi nditakhala ngati sindinakhaleko.

Ndikanangochokera m’mimba n’kupita kumanda.’

20 Kodi masiku anga si paja ndi ochepa?+ Iye andisiye,

Asiye kundiyang’anitsitsa kuti ndisangalaleko+ pang’ono

21 Ndisanapite. Ndikapita sindibweranso,+

Ndikapita kudziko lamdima wandiweyani,+

22 Kudziko lopanda kuwala, lamdima wandiweyani

Ndi lachisokonezo, losaona kuwala mofanana ndi malo amdima.”

11 Tsopano Zofari wa ku Naama+ anayankha kuti:

 2 “Kodi mawu ambirimbiri anganenedwe osayankhidwa?

Kapena kodi munthu wongodzitama angakhale wosalakwa?

 3 Kodi zolankhula zako zopanda pake zingachititse anthu kukhala chete?

Ndipo kodi upitirizabe kunyoza popanda wokudzudzula?+

 4 Komanso ukunena kuti, ‘Zimene ndimaphunzitsa + ndi zoyera,

Ndipo Mulungu amandiona kuti ndine woyera.’+

 5 Koma zikanakhala bwino Mulungu akanalankhula yekha

Ndi kukutsegulira pakamwa pake.+

 6 Bwenzi atakuuza chinsinsi cha nzeru,

Chifukwa zinthu za nzeru ndiponso zopindulitsa n’zambiri.

Komanso bwenzi utadziwa kuti Mulungu wachititsa kuti zolakwa zako zina ziiwalike.+

 7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,+

Kapena kodi ungadziwe mapeto a kukula kwa Wamphamvuyonse?

 8 N’zofika kutali kuposa kumwamba. Ungachite chiyani iwe?

N’zozama kuposa Manda.+ Ungadziwe chiyani iwe?

 9 N’zazitali kuposa kutalika kwa dziko lapansi,

N’zazikulu kuposa nyanja.

10 Iye akadutsa n’kupereka winawake,

N’kumuitanitsira bwalo, ndani angatsutsane naye?

11 Pakuti iye amawadziwa bwino amuna onyenga.+

Akaona zoipa zikuchitidwa, kodi sadzakhudzidwa nazo?

12 Ngati mbidzi yooneka ngati bulu ingabadwe munthu,

Ndiye kuti munthu wanzeru zoperewera angamvetse zinthu.

13 Ngati iweyo ungakonzekeretsedi mtima wako,

Ndi kutambasulira manja ako kwa iye,+

14 Ndiponso ngati m’manja mwako muli choipa, uchikankhire kutali,

Ndipo m’mahema ako musakhale zopanda chilungamo.

15 Ukatero, udzadzutsa nkhope yako osachita manyazi,+

Ndipo udzakhazikikadi, sudzachita mantha.

16 Pakuti iweyo udzaiwala mavuto.

Ndipo udzawakumbukira ngati madzi amene anadutsa.

17 Masiku a moyo wako+ adzakhala owala kuposa masana.

Usiku udzakhala ngati m’mawa.+

18 Udzalimba mtima chifukwa chakuti pali chiyembekezo.

Udzayang’anayang’ana paliponse mosamala, ndipo udzagona mopanda mantha.+

19 Ndithu udzadziwongola popanda aliyense wokuopsa.

Anthu ambiri adzakupangira zinthu zokuchititsa kuwakomera mtima.+

20 Maso a oipa sadzaonanso,+

Ndipo malo othawirako sadzawapeza.+

Chiyembekezo chawo chidzakhala imfa.”+

12 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Zoonadi, amuna inu ndinu anthu,

Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.+

 3 Inenso ndili ndi zolinga zabwino+ ngati inuyo.

Si ine wonyozeka kwa inu,+

Ndipo ndani amene alibe zinthu ngati zimenezi?

 4 Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu anzanga,+

Ndakhala munthu woitana kwa Mulungu kuti amuyankhe.+

Munthu wolungama ndi wosalakwa wakhala choseketsa.

 5 Amene ali pa mtendere amanyoza tsoka n’kumaganiza kuti+

Limagwera okhawo amene mapazi awo amaterereka.+

 6 Mahema a anthu olanda amakhala opanda nkhawa,+

Ndipo anthu okwiyitsa Mulungu amakhala pa mtendere

Wofanana ndi wa munthu amene watenga mulungu* m’manja mwake.+

 7 Koma funsa nyama zoweta ndipo zikulangiza.+

Komanso zouluka zam’mlengalenga, ndipo zikuuza.+

 8 Kapena chita chidwi ndi dziko lapansi, ndipo likulangiza.+

Nsomba za m’nyanja+ zikuuza.

 9 Ndani pa zonsezi sadziwa bwino

Kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?+

10 Iye amene moyo+ wa aliyense uli m’dzanja lake,

Ndiponso mzimu wa anthu onse.+

11 Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu+

Ngati mmene m’kamwa+ mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya?

12 Kodi okalamba si paja amakhala ndi nzeru,+

Ndipo amene akhala masiku ambiri si paja amamvetsa zinthu?

13 Iye ali ndi nzeru ndi mphamvu.+

Amapereka malangizo ndipo amamvetsa zinthu.+

14 Iyetu amagwetsa zinthu kuti zisamangidwe,+

Zimene iye watseka, palibe munthu amene angazitsegule.+

15 Amaletsa madzi ndipo amauma,+

Amawatumiza ndipo madziwo amasintha dziko lapansi.+

16 Iye ali ndi mphamvu ndi nzeru zopindulitsa.+

Kwa iye kuli wochimwa mosazindikira ndi wochimwitsa ena.+

17 Amachititsa alangizi kuyenda opanda nsapato,+

Ndipo oweruza amawachititsa misala.

18 Zingwe za mafumu amazimasula,+

Ndipo amawamanga lamba m’chiuno.

19 Amachititsa ansembe kuyenda opanda nsapato,+

Ndipo amene akhazikika amawawononga.+

20 Okhulupirika, iye amawakhalitsa chete,

Ndipo amuna okalamba, iye amawachotsera nzeru.

21 Iye amanyoza anthu olemekezeka,+

Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu.

22 Amavundukula zinthu zozama zimene zinali pamdima,+

Ndipo amaunika pamdima wandiweyani.

23 Amapatsa mphamvu mitundu kuti aiwononge.+

Amafutukula mitundu kuti aichotse.

24 Amachotsa nzeru za atsogoleri a anthuwo,

Kuti iwo aziyendayenda kumalo kopanda kanthu,+ kumene kulibe njira.

25 Iwo amafufuzafufuza mu mdima+ mopanda kuwala,

Kuti awachititse kuyendayenda ngati munthu woledzera.+

13 “Tamverani! Zonsezi maso anga aziona,

Ndipo khutu langa lamva ndi kuziganizira.

 2 Zimene amuna inu mukuzidziwa, inenso ndikuzidziwa bwino.

Si ine wotsika kwa inu.+

 3 Komabe ndikanakonda kulankhula ndi Wamphamvuyonse,+

Ndikanasangalala ndikanatsutsana ndi Mulungu.

 4 Koma amuna inu ndinu onamizira anzanu.+

Nonsenu ndinu madokotala opanda phindu.+

 5 Zikanakhala bwino mukanangokhala chete,

Pamenepo mukadakhala anthu anzeru.+

 6 Imvani mfundo zanga zotsutsana nanu,+

Ndipo tcherani khutu kuchonderera kwa milomo yanga.

 7 Kodi amuna inu mulankhula zopanda chilungamo m’malo mwa Mulungu?

Mulankhula zachinyengo m’malo mwa iye?+

 8 Kodi mum’kondera iyeyo?+

Kapena kodi mulimbana ndi Mulungu woona m’khoti?

 9 Kodi zingakhale bwino kuti iye akufufuzeni?+

Kapena mungam’pusitse ngati mmene mungapusitsire munthu?

10 Iye adzakudzudzulani ndithu,+

Mukadzayesera kuchita zinthu zokondera mwakabisira.+

11 Kodi kulemekezeka kwake sikudzakuchititsani mantha?

Kodi iye sadzakuchititsani kuti muope?+

12 Mawu anu osaiwalika ndiwo miyambi yopanda pake ngati phulusa.

Mayankho anu odziteteza ali ngati zishango zadothi.+

13 Khalani chete pamaso panga, kuti ineyo ndilankhule.

Kenako chilichonse chondifikira chindifikire.

14 N’chifukwa chiyani ndikuika moyo wanga pachiswe,*

Ndiponso kuika moyo wanga m’dzanja langa?+

15 Ngati iye atandipha, kodi sindidzadikirira?+

Komabe ndingatsutsane naye pamasom’pamaso za njira zanga.

16 Komanso iye adzakhala chipulumutso changa,+

Chifukwa pamaso pake sipadzafika wampatuko.+

17 Mumvetsere mawu anga mosamala,+

Ndipo zolankhula zanga zikhale m’makutu mwanu.

18 Ndimvereni, ndabweretsa mlandu wofunika kuuzenga.+

Ineyo ndikudziwa bwino kuti sindinalakwe.

19 Ndani amene angatsutsane nane?+

Ngati ndingakhale chete osalankhula, ndikhoza kungofa.

20 Pali zinthu ziwiri zokha zoti musandichitire.

Mukatero sindidzabisala pamaso panu.+

21 Ikani dzanja lanu kutali ndi ine,

Ndipo kuopsa kwanu kusandichititse mantha.+

22 Muitane kuti ine ndivomere.

Kapena ndilankhule ndipo inu mundiyankhe.

23 Kodi ine ndinalakwa ndiponso kuchimwa mwa njira yanji?

Ndidziwitseni kulakwa kwanga ndiponso tchimo langa.

24 N’chifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,+

N’kunditenga ine ngati mdani wanu?+

25 Kodi mukuopseza ine tsamba lachabechabe louluzika ndi mphepo?

Kapena mukuthamangitsa ine udzu wouma wachabechabe?

26 Pakuti inu mukupitiriza kundilembera zinthu zowawa,+

Ndipo mukundipatsa zotsatira za zolakwa zimene ndinachita ndili mnyamata.+

27 Ndiponso simukuchotsa mapazi anga m’matangadza,+

Ndipo mumayang’anitsitsa njira zanga zonse.

Mapazi anga mumawalembera malire.

28 Ine* ndili ngati chinthu chowola chimene chimatha.+

Ngati chovala chimene njenjete* zimadya.+

14 “Munthu wobadwa kwa mkazi,+

Amakhala ndi moyo waufupi,+ wodzaza ndi masautso.+

 2 Amaphuka ngati duwa n’kuthotholedwa.+

Amathawa ngati mthunzi+ ndipo sakhalaponso.

 3 Ameneyu mwamuyang’ana ndi diso lanu,

Ndipo ine mukundizenga mlandu.+

 4 Ndani anabadwa ali woyera kuchokera mwa munthu wodetsedwa?+

Palibe ndi mmodzi yemwe.

 5 Masiku a munthu ndi odziwika,+

Ndipo chiwerengero cha miyezi yake chili ndi inu.

Mwamuikira lamulo kuti asalipitirire.

 6 Siyani kumuyang’anitsitsa kuti apumule,+

Mpaka apeze chisangalalo ngati mmene amachitira waganyu pakutha pa tsiku.

 7 Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo.

Ukadulidwa umaphukanso,+

Ndipo nthambi yake idzakhalapo mpaka kalekale.

 8 Muzu wake ukakalamba m’nthaka,

Ndipo chitsa chake chikafa m’fumbi,

 9 Ukadzangomva fungo la madzi udzaphukira,+

Ndipo udzamera nthambi ngati mtengo watsopano.+

10 Koma mwamuna wamphamvu amafa ndipo amagona pansi atagonjetsedwa.

Munthu wochokera kufumbi amatha. Kodi ali kuti?+

11 Madzi amatha m’nyanja,

Ndipo madzi a mumtsinje amaphwa n’kuuma.+

12 Anthu nawonso amagona pansi osadzuka.+

Sadzadzuka mpaka kumwamba kutachoka,+

Sadzadzutsidwa ku tulo tawo.+

13 Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda,+

Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka,

Mukanati mundiikire nthawi+ n’kudzandikumbukira.+

14 Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?+

Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza,+

Mpaka mpumulo wanga utafika.+

15 Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha.+

Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.

16 Panopa mukungokhalira kuwerenga mmene mukudutsa mapazi anga,+

Mukungoyang’ana machimo anga basi.+

17 Kulakwa kwanga mwakutsekera m’thumba,+

Ndipo mwamata machimo anga ndi zomatira.

18 Ngakhale phiri limagwa n’kugumukagumuka,

Ngakhale thanthwe limasunthidwa pamalo ake.

19 Madzi amaperesa ngakhale miyala.

Akamathamanga amakokolola dothi la padziko lapansi.

Inunso mwawononga chiyembekezo cha munthu.

20 Mumamugonjetsa kwamuyaya, moti amachoka.+

Mumapundula nkhope yake n’kumuthamangitsa.

21 Ana ake amalemekezedwa, koma iye sadziwa zimenezo.+

Iwo amakhala opanda pake, koma iye sawaganizira.

22 Mnofu wake umawawa adakali nawo,

Ndipo moyo wake umapitiriza kulira udakali mwa iye.”

15 Tsopano Elifazi wa ku Temani anayankha kuti:

 2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi nzeru zopanda pake,+

Kapena angadzaze mimba yake ndi mphepo ya kum’mawa?+

 3 Kungodzudzula ndi mawu n’kopanda ntchito,

Ndipo mawu ndi osathandiza paokha.

 4 Koma chifukwa cha iweyo kuopa Mulungu kwatha,

Ndipo ukupeputsa phindu losinkhasinkha pamaso pa Mulungu.

 5 Chifukwa zolakwa zako zimaphunzitsa pakamwa pako zoti palankhule,

Ndipo umasankha lilime la akathyali.

 6 Pakamwa pako m’pamene pakunena kuti ndiwe wolakwa, osati ine,

Ndipo milomo yako ikuyankha motsutsana nawe.+

 7 Kodi iwe unali munthu woyamba kubadwa?+

Kodi unabadwa ndi zowawa za pobereka, mapiri asanakhaleko?+

 8 Kodi umamvetsera nkhani zachinsinsi za Mulungu?+

Ndipo kodi umaona kuti iwe wekha ndiye wanzeru?

 9 Ukudziwa chiyani chimene ife sitikudziwa?+

Ndipo umamvetsa chiyani chimene ifeyo tilibe?

10 Aimvi ndi okalamba ali pakati pathu,+

Omwe ali akale kuposa bambo ako.

11 Kodi chitonthozo cha Mulungu sichikukukwanira?

Kapena kulankhula nawe mawu odekha sikunakukwanire?

12 N’chifukwa chiyani mtima wako ukudzikweza?

Ndipo n’chifukwa chiyani maso ako akuwala?

13 Pakuti mtima wako watembenukira Mulungu,

Ndipo iwe watulutsa mawu oipa ndi pakamwa pako.

14 Kodi munthu ndani kuti akhale woyera?+

Kapena munthu wobadwa kwa mkazi kuti akhale wosalakwa?

15 Iyetu alibe chikhulupiririro mwa angelo* ake,+

Ndipo kumwamba si koyera m’maso mwake.+

16 Nanga kuli bwanji munthu wonyansa ndi woipa,+

Munthu yemwe amamwa zosalungama ngati madzi?

17 Inetu ndikuuza. Tamvera!+

Dikira ndikuuze zimene ndaziona,

18 Zimene anzeru+ amanena,

Ndiponso zimene sanabise, zochokera kwa makolo awo.

19 Dziko linaperekedwa kwa iwo okha,

Ndipo palibe mlendo amene anadutsa pakati pawo.

20 Woipa amavutika ndi zowawa masiku ake onse,

Ngakhale pa zaka zonse zimene zasungidwira wolamulira wankhanza.

21 Woipayo amamva phokoso la zoopsa m’makutu ake,

Pa nthawi yamtendere wolanda amam’bwerera.+

22 Iye sakhulupirira kuti adzatuluka mu mdima,+

Ndipo akudikira lupanga.

23 Amayendayenda pofunafuna chakudya. Kodi chili kuti?+

Akudziwa bwino kuti tsiku la mdima+ layandikira.

24 Zowawa ndi zozunza zimangokhalira kumuchititsa mantha.+

Zimamugonjetsa ngati mfumu yomwe yakonzekera nkhondo.

25 Popeza amatambasula dzanja lake motsutsana ndi Mulungu,

Ndipo amayesera kuti akhale wamkulu kuposa Wamphamvuyonse,+

26 Popeza iye amalimbana ndi Mulungu mwaliuma,

Ndi zishango zake zokhala ndi mfundo zochindikala,

27 Popeza nkhope yake yaphimbika ndi mafuta a m’thupi mwake,

Ndipo wanenepa m’chiuno mwake,+

28 Iye amakhala m’mizinda imene idzafafanizidwe,

M’nyumba zimene anthu sadzapitiriza kukhalamo,

Zimene mosakayikira zidzakhala milu ya miyala.

29 Iye sadzalemera ndipo chuma chake sichidzachuluka.

Zinthu zimene adzatenge kwa iwo, sadzazimwaza padziko lapansi.+

30 Iye sadzachoka mu mdima,

Moto udzaumitsa nthambi yake,

Ndipo adzachotsedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwa Mulungu.+

31 Iye asakhulupirire zopanda pake n’kusocheretsedwa,

Chifukwa zopanda pake n’zimene zidzakhale malipiro ake.

32 Zimenezi zidzakwaniritsidwa tsiku la woipayo lisanafike,

Ndipo mphukira yake sidzakula mosangalala.+

33 Adzathothola mphesa zake zosapsa ngati mtengo wa mpesa,

Ndipo adzayoyola maluwa ake ngati mtengo wa maolivi.

34 Pakuti msonkhano wa ampatuko ndi wopanda phindu,+

Ndipo moto uyenera kunyeketsa mahema a anthu aziphuphu.+

35 Iwo amatenga pakati pamavuto n’kubereka zopweteka,+

Ndipo mimba yawo imakonza zachinyengo.”

16 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Ndamva zinthu zambiri ngati zimenezi.

Nonsenu ndinu otonthoza onditopetsa!+

 3 Kodi mawu opanda pakewa saatha?+

Kapena chikukupwetekani n’chiyani kuti muziyankha?

 4 Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu,

Moyo wanu ukanakhala ngati mmene ulili moyo wanga,

Kodi ndikanalankhula mawu ogometsa okunenani?+

Ndipo kodi ndikanakupukusirani mutu?+

 5 Ndikanakulimbikitsani ndi mawu a m’kamwa mwanga,+

Ndipo chitonthozo cha milomo yanga chikanachepetsa . . .

 6 Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa.+

Ndikasiya kutero, n’chiyani chikundichokera?

 7 Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+

Wawononga onse osonkhana nane.

 8 Komanso inu mwandigwira. Umenewu wakhala umboni,+

Mwakuti kuwonda kwanga kwandiukira ndipo kukuchitira umboni pankhope panga.

 9 Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula. Iye ali nane chidani+

Ndipo akundikukutira mano.+

Mdani wanga akundiyang’ana ndi diso lozonda.+

10 Iwo ayasamula kukamwa kwawo kuti andimeze.+

Andimenya mbama ndi mnyozo.

Asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+

11 Mulungu wandipereka kwa anyamata,

Ndipo wandiponya mwamphamvu m’manja mwa oipa.+

12 Ine ndinali pa mtendere koma iye anandikhutchumula.+

Anandigwira kumbuyo kwa khosi n’kundimenyetsa pansi,

Ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.

13 Anthu ake oponya mivi ndi uta+ andizungulira.

Iye wandiboola impso+ koma osamva chisoni,

Wakhuthulira ndulu yanga pansi.

14 Iye akungokhalira kundiboola ngati mpanda.

Akundithamangira ngati mmene amachitira wamphamvu.+

15 Khungu langa ndalisokera ziguduli*+ zoti livale,

Ndipo ndaika nyanga yanga m’fumbi.+

16 Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+

Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,+

17 Chonsecho manja anga sanachite zachiwawa,

Ndipo pemphero langa ndi loyera.+

18 Iwe dziko lapansi, usaphimbe magazi anga.+

Pasapezeke malo osungira kulira kwanga.

19 Komanso, wochitira umboni za ine ali kumwamba,

Ndipo mboni yanga ili m’mwamba.+

20 Anzanga asanduka ondilankhulira otsutsana nane.+

Diso langa lakhala likuyang’ana kwa Mulungu osagona.+

21 Chiweruzo chiperekedwe pakati pa mwamuna wamphamvu ndi Mulungu,

Mofanana ndi pakati pa mwana wa munthu ndi mnzake.+

22 Chifukwa pangotsala zaka zochepa,

Ndipo ndidzapita ndi njira yomwe sindidzabwerera nayonso.+

17 “Mzimu wanga wasweka,+ masiku anga atha.

Kwanga n’kumanda.+

 2 Ndithu, onyoza andizungulira,+

Ndipo diso langa likuyang’anitsitsa khalidwe lawo lopanduka.

 3 Chonde, mundisungire chotsimikizira changa.+

Palinso ndani amene angagwirane nane chanza+ monga chikole?

 4 Pakuti mtima wawo mwauchititsa kuti ukhale wopanda nzeru.+

N’chifukwa chake simukuwakweza.

 5 Munthu angauze anzake kuti atengepo mbali yawo,

Koma maso a ana ake adzachita mdima.+

 6 Iye wandisandutsa mwambi+ wa anthu,

Mwakuti ndakhala munthu womulavulira kumaso.+

 7 Chifukwa cha kuzunzika, diso langa layamba kuchita mdima.+

Ziwalo zanga zonse zakhala ngati mthunzi.

 8 Anthu owongoka mtima akuyang’ana zimenezi modabwa,

Ndipo ngakhale munthu wosalakwa wakwiyira wopanduka.

 9 Wolungama akuyendabe panjira yake,+

Ndipo wa manja oyera+ akungowonjezeka mphamvu.+

10 Komabe, amuna nonsenu mungathe kuyambiranso kundinena. Chotero pitirizani,

Chifukwa sindikuonapo wanzeru pakati panu.+

11 Masiku anga atha,+ zolinga zanga zasokonezedwa,+

Zofuna za mtima wanga zasokonezedwa.

12 Anzanga akungokhalira kunena zabodza m’malo monena zoona.*+ Iwo akunena kuti:

‘Kuwala kuli pafupi, pamene ine ndikungoona mdima wokhawokha.’

13 Ndikapitiriza kudikira, ku Manda kukhala kunyumba kwanga.+

Ndidzayala bedi langa mu mdima.+

14 Ndidzaitana dzenje+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’

Kwa mphutsi+ ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’

15 Chotero, kodi chiyembekezo changa chili kuti?+

Kodi pali amene akuona kuti ine ndili ndi chiyembekezo?

16 Iwo adzatsikira ku Manda otsekedwa ndi zitsulo,

Pa nthawi imene tonsefe tidzatsikira limodzi kufumbi.”+

18 Tsopano Bilidadi wa ku Shuwa anayankha kuti:

 2 “Kodi zikutengerani nthawi yaitali bwanji anthu inu kuti musiye kulankhula?

Muyenera kumvetsa kuti kenako tilankhule.

 3 N’chifukwa chiyani mukutiona ngati zinyama,+

Ndiponso mukutiona ngati odetsedwa m’maso mwanu?

 4 Iwe amene ukukhadzula moyo wako mumkwiyo wako,

Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe?

Kapena mwala ungasunthe pamalo ake chifukwa cha iwe?

 5 Kuwala kwa oipa kudzazimitsidwa,+

Ndipo moto wake sudzawala.

 6 Kuwala kudzazima m’hema wake,+

Nyale yake idzazimitsidwa mmenemo.

 7 Adzasiya kuyenda mwamphamvu n’kuyamba kuyenda mopanikizika.

Ngakhale malangizo ake adzam’gwetsa.+

 8 Pakuti adzakodwa mu ukonde ndi mapazi ake,

Ndipo adzayenda m’zingwe za ukonde.+

 9 Msampha wam’gwira chidendene.+

Khwekhwe+ lam’kola.

10 Chingwe choti chim’kole chabisidwa pansi,

Ndipo msampha woti um’gwire uli panjira yake.

11 Paliponse, zoopsa zadzidzidzi zimamuchititsa mantha,+

Ndipo zimamuthamangitsa zili pafupi naye kwambiri.

12 Mphamvu zake zimachepa,

Ndipo tsoka+ limakhala likudikira kuti limuyendetse motsimphina.

13 Mwana woyamba wa imfa azidzanyotsola khungu la munthuyo n’kumadya.

Iye adzadya ziwalo zake.

14 Zinthu zimene amazidalira zidzachotsedwa m’hema wake,+

Ndipo zidzapita naye kwa mfumu ya zoopsa.

15 M’hema mwake mudzakhala chinthu chimene si chake.

Sulufule+ adzawazidwa pamalo ake okhala.

16 Pansi, mizu yake idzauma.+

Pamwamba, nthambi yake idzafota.

17 Dzina lake silidzatchulidwanso padziko lapansi,+

Ndipo mumsewu simudzakhala dzina lake.

18 Adzamuchotsa powala n’kumukankhira kumdima.

Adzamuthamangitsa panthaka ya padziko lapansi.

19 Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,+

Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala monga mlendo.

20 Pa tsiku la tsoka lake anthu a Kumadzulo adzayang’ana modabwa,

Ndipo anthu a Kum’mawa adzanjenjemera.

21 Izi n’zimene zimachitikira malo okhala munthu woipa,

Ndipo awa ndiwo malo a munthu wosadziwa Mulungu.”

19 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Kodi amuna inu musautsa moyo wanga mpaka liti,+

Ndi kundilasa ndi mawu?+

 3 Mwandidzudzula maulendo 10 onsewa.

Kodi simukuchita manyazi kuti mukundizunza?+

 4 Ngati ndachita cholakwa,+

Cholakwa changacho chikhala ndi ine.

 5 Ngati amuna inu mukudzikweza polimbana nane,+

Ndipo mukuonetsa kuti chitonzo changa n’chondiyenerera,+

 6 Dziwani kuti Mulungu mwiniwakeyo ndi amene wandisocheretsa,

Ndipo wandizunguliza ndi ukonde wake wosakira nyama.+

 7 Inetu ndakhala ndikukuwa kuti, ‘Chiwawa!’ koma palibe woyankha.+

Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.+

 8 Iye watchinga njira yanga ndi mpanda wamiyala+ mwakuti sindingathe kudutsa.

Ndiponso waika mdima panjira zanga.+

 9 Iye wandichotsera ulemerero wanga,+

Wandilanda chisoti chaulemu cha kumutu kwanga.

10 Akundikokera pansi mbali zonse, ine n’kuchoka.

Wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.

11 Mkwiyo wake nawonso wandiyakira,+

Ndipo akungondiona ngati ndine mdani wake.

12 Asilikali ake agwirizana n’kubwera kudzamanga njira yawo kuti alimbane nane,+

Ndipo azungulira hema wanga.

13 Iye waika abale anga enieni kutali ndi ine,+

Ndipo ngakhale anthu ondidziwa andisiya.

14 Anzanga apamtima anditaya.+

Anthu amene ndinali kuwadziwa andiiwala,

15 Iwo amene anali kukhala m’nyumba mwanga monga alendo.+ Akapolo anga aakazi akukhala ngati sakundidziwa.

Ndakhala mlendo weniweni m’maso mwawo.

16 Ndaitana wantchito wanga koma sakundiyankha.

Ndikukhalira kumuchonderera ndi pakamwa panga kuti andimvere chisoni.

17 Mpweya wanga wasanduka wonyansa kwa mkazi wanga,+

Ndipo ndakhala wonunkha kwa ana obadwa kwa mayi anga.

18 Nawonso anyamata ang’onoang’ono andikana.+

Ndikaimirira, amayamba kunditsutsa.

19 Amuna onse amene anali anzanga apamtima akudana nane,+

Ndipo amene ndinali kuwakonda anditembenukira.+

20 Ndangotsala mafupa okhaokha,+

Ndipo pang’onong’ono n’kanafa.*

21 Ndichitireni chifundo anzanganu, ndichitireni chifundo,+

Chifukwa dzanja la Mulungu landikhudza.+

22 N’chifukwa chiyani amuna inu mukungokhalira kundizunza ngati mmene akuchitira Mulungu?+

Kodi simunatope ndi kundinenera zoipa?

23 Tsopano ndikulakalaka mawu anga akanalembedwa!

Ndithu akanalembedwa m’buku!

24 Akanalembedwa ndi chitsulo chogobera+ n’kukhuthulirapo mtovu,

Akanalembedwa pathanthwe mochita kugoba kuti akhale kwamuyaya.

25 Ineyo ndikudziwa bwino kuti wondiwombola+ ali moyo,

Ndipo adzabwera pambuyo panga n’kuimirira+ pafumbi.

26 Pambuyo pa khungu langa limene alisenda, zidzakhala chonchi.

Koma ndili wowonda choncho, ndidzaona Mulungu.

27 Inetu ndidzamuona.+

Maso angawa, osati a mlendo winawake, adzamuonadi Mulungu.*

Impso zanga zasiya kugwira ntchito mkati mwanga.

28 Pakuti amuna inu mukunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani tikungokhalira kumuzunza?’+

Chonsecho muzu wa nkhaniyo ndine.

29 Opani lupanga,+

Chifukwa lupanga limaukira ochita zoipa,

Kuti amuna inu mudziwe kuti kuli woweruza.”+

20 Tsopano Zofari wa ku Naama anayankha kuti:

 2 “N’chifukwa chake malingaliro anga osautsa akundiyankha,

Chifukwa cha mkwiyo wa mumtima mwanga.

 3 Ndikumva mawu ondinyoza,

Ndipo munthu wa mtima wopanda nzeru ngati zimene ine ndili nazo, akundiyankha.

 4 Kodi wakhala ukudziwa zimenezi kuyambira kalekale,

Kuyambira pamene munthu anaikidwa padziko lapansi?+

 5 Kuti mfuu yachisangalalo ya anthu oipa sikhalitsa,+

Ndiponso kuti kusangalala kwa wampatuko kumakhala kwa kanthawi?

 6 Ngakhale kuti ulemerero wake umafika mpaka kumwamba,+

Ndipo mutu wake umafika m’mitambo?

 7 Adzatheratu mofanana ndi ndowe zake.+

Amene ankamuona adzati, ‘Ali kuti kodi?’+

 8 Iye adzauluka ngati loto, ndipo sadzam’peza.

Adzathamangitsidwa ngati masomphenya a usiku.+

 9 Diso limene lamuona silidzam’penyanso,+

Ndipo malo ake sadzamuonanso.+

10 Ana ake adzafunafuna kuti anthu onyozeka awachitire chifundo.

Manja ake adzabweza zinthu zake zamtengo wapatali.+

11 Mafupa ake anali odzaza ndi mphamvu zake zaunyamata,

Koma adzagona nazo limodzi m’fumbi.+

12 Ngati zoipa zimatsekemera* m’kamwa mwake,

Ngati amazibulumunya kuseri kwa lilime lake,

13 Ngati amazikonda ndipo sazisiya,

Ngati amazivumata m’kamwa mwake,

14 Chakudya chake chidzasintha m’matumbo mwake.

Chidzakhala poizoni wa mamba m’thupi mwake.

15 Wameza chuma, koma adzachisanza.

Mulungu adzachithamangitsa m’mimba mwake.

16 Adzayamwa poizoni wa mamba,

Lilime la mphiri lidzamupha.+

17 Sadzaona ngalande za madzi,+

Mitsinje yosefukira ndi uchi ndi mafuta a mkaka.

18 Adzabweza chuma chimene anachipeza ndipo sadzachimeza.

Chumacho chidzakhala ngati chuma chochokera ku malonda ake chimene sadzachidyerera.+

19 Pakuti watswanyatswanya onyozeka n’kuwasiya,

Walanda nyumba imene sanamange,+

20 Sadzapeza mtendere m’mimba mwake.

Zinthu zake zabwinozabwino sizidzam’pulumutsa.+

21 Palibe chimene chatsala choti ameze,

N’chifukwa chake ulemerero wake sudzakhalitsa.

22 Chuma chake chitafika pachimake, adzakhala ndi nkhawa.+

Tsoka lidzamugwera ndi mphamvu zonse.

23 Mulungu atumize mkwiyo wake woyaka moto pa iye,

N’kuudzaza m’mimba mwake.+

Auvumbitsire pa iye kuti ufike mpaka m’matumbo mwake.

24 Iye adzathawa+ zida zankhondo zachitsulo.

Uta wa mkuwa udzamulasa.

25 Muvi udzatulukira kumsana kwake,

Ndipo chida chonyezimira chidzaboola ndulu yake.+

Zida zoopsa zidzam’pweteka.+

26 Zinthu zake zapamtima zidzakumana ndi mdima wokhawokha.

Moto wopanda woukolezera udzamunyeketsa.+

Munthu wotsala muhema wake zinthu zidzamuipira.

27 Kumwamba kudzaulula cholakwa chake,+

Ndipo dziko lapansi lidzamuukira.

28 Mvula yamphamvu idzakokolola nyumba yake.

Zinthu zambiri zidzam’gwera pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu.+

29 Ili ndilo gawo la munthu woipa kuchokera kwa Mulungu,+

Cholowa chake chimene Mulungu wam’patsa.”

21 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Amuna inu, mvetserani mwatcheru mawu anga.

Zimenezi zikhale zokutonthozani.

 3 Ndilezereni mtima kuti ndilankhule.

Ndikamaliza kulankhula, aliyense wa inu akhoza kuyamba kunyoza.+

 4 Kodi ineyo ndauza munthu nkhawa zanga?

Kapena n’chifukwa chiyani mzimu wanga sukukwiya?

 5 Tembenuzirani nkhope zanu kwa ine n’kundiyang’ana modabwa,

Ndipo muike dzanja lanu pakamwa.+

 6 Ndikakumbukira, zikundisokoneza maganizo,

Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.

 7 N’chifukwa chiyani oipa amakhalabe ndi moyo,+

Amakalamba komanso amalemera kwambiri?+

 8 Ana awo akhazikika nawo limodzi pamaso pawo,

Ndiponso mbadwa zawo zakhazikika iwo akuona.

 9 Nyumba zawo zili pa mtendere, zosaopa chilichonse,+

Ndipo ndodo ya Mulungu sili pa iwo.

10 Ng’ombe zawo zamphongo zimapereka bere, ndipo siziwononga mphamvu zobereketsa.

Ng’ombe zawo zazikazi zimabereka+ ndipo sizibereka ana akufa.

11 Iwo amalola ana awo kutuluka panja ngati nkhosa,

Ndipo anawo amakhala akudumphadumpha pabwalo.

12 Iwo amafuula nthawi zonse poimba maseche ndi azeze.+

Amakhala akusangalala poimba zitoliro.

13 Masiku awo onse amakhala moyo wabwino,+

Ndipo posakhalitsa amatsikira ku Manda.

14 Amauza Mulungu woona kuti, ‘Chokani kwa ife!+

Sitikufuna kudziwa njira zanu.+

15 Kodi Wamphamvuyonse ndani kuti tim’tumikire?+

Ndipo kulankhula naye kungatipindulitse chiyani?’+

16 Komatu, ulemerero wawo saupeza chifukwa cha mphamvu zawo.+

Malangizo a anthu oipa atalikirana nane.+

17 Kodi nyale ya oipa imazimitsidwa kangati?+

Ndipo tsoka lawo limawagwera kangati?

Kodi ndi kangati pamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?+

18 Kodi iwo amakhala ngati udzu wouluzika ndi mphepo?+

Kapena ngati mankhusu* ouluka ndi mphepo yamkuntho?

19 Zoipa zimene munthu anachita, Mulungu adzazisungira ana ake omwe,+

Adzam’patsa mphoto yake, ndipo iye adzaidziwa.+

20 Maso ake adzaona kuwola kwake,

Ndipo iye adzamwa mkwiyo wa Wamphamvuyonse.+

21 Kodi adzatha kusangalala ndi ana ake iyeyo atapita,

Chiwerengero cha miyezi yake chitadulidwa pakati?+

22 Kodi adzaphunzitsa Mulungu nzeru,+

Pamene Mulunguyo azidzaweruza anthu apamwamba?+

23 Munthu ameneyo adzafa ali wokhutira.+

Adzafa ali pa mtendere ndiponso wosatekeseka.

24 Ntchafu zake zitadzaza mafuta,

Ndiponso mafuta a m’mafupa mwake akadali ofewa.

25 Winanso adzafa ali wokwiya,

Asanadye zinthu zabwino.+

26 Iwo adzagona limodzi m’fumbi,+

Ndipo mphutsi zidzawakuta.+

27 Inetu ndikudziwa bwino maganizo anu amuna inu,

Ndiponso zachiwawa zimene mungapangane kuti mundichitire.+

28 Popeza mukuti, ‘Kodi nyumba ya wolemekezeka ili kuti,

Ndipo hema wa oipa ali kuti? Kodi malo awo okhala ali kuti?’+

29 Kodi simunafunse anthu oyenda m’misewu,

Ndipo simuonetsetsa zizindikiro zawo,

30 Kuti pa tsiku la tsoka woipa amapulumuka,+

Ndipo pa tsiku la mkwiyo amawomboledwa?

31 Ndani angamuuze za njira yake pamasom’pamaso,+

Ndipo ndani adzam’patse mphoto ya zimene wachita?+

32 Iyeyo anthu adzam’tengera kumanda,+

Ndipo anthu adzachezera pamanda ake.

33 Kwa iye zibuma za dothi lochokera m’chigwa* zidzakhala zotsekemera.+

Pambuyo pake adzakoka anthu onse,+

Ndipo amene anapita iye asanapite n’ngosawerengeka.

34 Choncho, amuna inu mukungodzivuta poyesa kunditonthoza,+

Ndipo mayankho anu ndi mabodza okhaokha.”

22 Tsopano Elifazi wa ku Temani anayankha kuti:

 2 “Kodi mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu?+

Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye?

 3 Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?+

Kapena amapindula chilichonse chifukwa chakuti suchita cholakwa?+

 4 Kodi adzakudzudzula chifukwa choopa Mulungu?

Kodi adzapita nawe kwa woweruza?+

 5 Kodi kuipa kwako sikwapitirira kale muyezo?+

Kodi zolakwa zako sizidzatha?

 6 Umalanda abale ako chikole popanda chifukwa,+

Umalanda zovala anthu osauka n’kuwasiya ali maliseche.

 7 Wotopa sum’patsa madzi akumwa,

Ndipo wanjala sum’patsa chakudya.+

 8 Munthu wamphamvu, dziko ndi lake.+

Ndipo munthu amene amam’kondera amakhala mmenemo.

 9 Akazi amasiye wawabweza chimanjamanja,

Ndipo wafooketsa manja a ana amasiye.*+

10 N’chifukwa chake misampha ya mbalame yakuzungulira,+

Ndipo ukusokonezeka ndi zoopsa zadzidzidzi.

11 N’chifukwa chake pali mdima, moti sungathe kuona,

Ndipo madzi osefukira akumiza.

12 Kodi Mulungu si wapamwamba kuposa kumwamba?+

Onanso kuti nyenyezi+ zonse zili m’mwamba.

13 Komabe iwe wanena kuti: ‘Mulungu akudziwa chiyani?

Kodi angathe kuweruza pali mdima wandiweyani?

14 Mitambo imamutchingira malo moti saona,

Ndipo iye amayenda pamwamba pa thambo.’

15 Kodi upitiriza kuyenda panjira yakalekale

Imene anthu ochita zoipa anayendamo,

16 Anthu amene anatengedwa nthawi yawo isanakwane,+

Amene maziko+ awo amakhuthulidwa ngati madzi a mumtsinje,

17 Ndiponso amene amauza Mulungu woona kuti: ‘Tichokereni!+

Kodi Wamphamvuyonse angatichite chiyani?’

18 Chonsecho iye wadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,+

Ndipo malangizo a anthu oipa ali kutali ndi ine.+

19 Olungama adzaona chiwonongeko chawo n’kusangalala,+

Ndipo wosalakwa adzawaseka kuti:

20 ‘Zoonadi adani athu afafanizidwa,

Ndipo zimene azisiya, moto udzazinyeketsa.’

21 Um’dziwe bwino Mulungu ndi kukhala naye pa mtendere.

Ukatero zinthu zabwino zidzabwera kwa iwe.

22 Tenga malamulo pakamwa pake,

N’kuika mawu ake mumtima mwako.+

23 Ukabwerera kwa Wamphamvuyonse,+ udzabwezeretsedwa mwakale.

Ukaika zosalungama kutali ndi hema wako,

24 Ndipo ukataya golide wako wamtengo wapatali m’fumbi,

Ukataya golide wa ku Ofiri+ m’miyala ya m’zigwa,*

25 Ndithu Wamphamvuyonse adzakhala golide wako wamtengo wapatali,

Ndiponso siliva wako wabwino kwambiri.+

26 Kenako udzasangalala kwambiri ndi Wamphamvuyonse,+

Ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.+

27 Udzamudandaulira ndipo adzakumvera.+

Udzapereka kwa iye zimene unalonjeza.+

28 Zimene waganiza kuti uchite zidzatheka,

Ndipo kuwala kudzaunikira njira zako.+

29 Ukamalankhula modzitukumula udzachititsidwa manyazi.+

Koma iye adzapulumutsa wankhope yozyolika.+

30 Adzapulumutsa munthu wosalakwa,+

Ndipo iwe udzapulumutsidwa chifukwa chakuti manja ako ndi oyera.”+

23 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Ngakhale lero, sindikusangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Chotero ndikudandaula.+

Dzanja langa likulemera chifukwa chakuti ndikuusa moyo.

 3 Ndikanadziwa kumene ndingamupeze,+

Bwenzi nditapita kumalo kumene iye amakhala nthawi zonse.+

 4 Bwenzi nditapita pamaso pake ndi nkhani yoti aweruze.

M’kamwa mwanga bwenzi nditadzazamo mfundo zodziikira kumbuyo.

 5 Bwenzi nditadziwa mawu amene amanena pondiyankha,

Ndipo bwenzi nditaganizira zimene amandiuza.+

 6 Kodi bwenzi iye atalimbana nane ndi mphamvu zambiri?

Ayi ndithu! Iye akanandimvera.+

 7 Kumeneko, wowongoka mtima adzathetsa nkhani zake ndi iye,

Ndipo ine ndikanapulumuka kwa woweruza wanga mpaka kalekale.

 8 Ndikapita kum’mawa, iye kulibe.

Ndikabwerako, sindimuona.+

 9 Ndimapita kumanzere kumene iye akugwira ntchito, koma sindimuona.

Amatembenukira kudzanja lamanja, koma ine osamuona,

10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+

Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+

11 Mapazi anga amatsata mayendedwe ake.

Ndasunga njira yake, ndipo sindipatukapo.+

12 Sindisiya malamulo otuluka pakamwa pake.+

Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake+ kuposa zimene akufuna kuti ndichite.

13 Iye ali ndi maganizo amodzi, ndani angam’tsutse?+

Zimene moyo wake umalakalaka amazichita.+

14 Iye adzachita zonse zimene wandikonzera,+

Ndipo zinthu zoterezi n’zambiri kwa iye.

15 N’chifukwa chake ndikusokonezeka chifukwa cha iye.

Ndikaganizira za iye, ndikumachita mantha.+

16 Mulungu wachititsa mantha mtima wanga.+

Wamphamvuyonse wandisokoneza,+

17 Pakuti sindinaletsedwe kulankhula chifukwa cha mdima,

Kapenanso chifukwa chakuti mdima wandiweyani waphimba nkhope yanga.

24 “N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo,+

Ndipo n’chifukwa chiyani omudziwa sanaone masiku ake achiweruzo?+

 2 Pali anthu amene amasuntha malire,+

Iwo alanda gulu la ziweto kuti aziziweta.

 3 Amathamangitsa ngakhale bulu wamphongo wa ana amasiye,*

Amalanda ng’ombe yamphongo ya mkazi wamasiye ngati chikole.+

 4 Amapatutsa osauka panjira,+

Ndipo pa nthawi yomweyo ozunzika a padziko lapansi amakhala atabisala.

 5 Monga mbidzi+ m’chipululu,

Osaukawo amapita kukafunafuna chakudya.

Chipululu chimapatsa aliyense chakudya cha ana ake.

 6 M’munda wa munthu wina, osauka amakololamo chakudya cha ziweto,

Ndipo iwo amalanda msangamsanga zinthu za m’munda wa mpesa wa munthu woipa.

 7 Osaukawo amakhala usiku wonse ali maliseche,+

Amakhala pamphepo opanda chofunda.+

 8 Amanyowa ndi mvula yamkuntho ya m’mapiri,

Ndipo chifukwa chakuti alibe pobisala,+ amakupatira thanthwe.

 9 Oipa amalanda mwana wamasiye kum’chotsa pabere.+

Amatenga ngati chikole chovala chimene wozunzika wavala.+

10 Ozunzika amayenda opanda chovala,

Amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.+

11 Nthawi ya masana amakhala pakati pa migula ya m’minda.

Amaponda mphesa koma amakhala ndi ludzu.+

12 Anthu amene akufa amamveka kubuula kunja kwa mzinda,

Moyo wa anthu amene akufa chifukwa chovulala umafuula popempha thandizo,+

Ndipo Mulungu saziona ngati zolakwika.+

13 Oipawo amasonyeza kuti ali pakati pa opanduka omwe amatsutsana ndi kuwala.+

Iwo sanazindikire njira zake,

Ndipo sanakhale m’misewu yake.

14 Kukangocha, wakupha amadzuka

Kupita kukapha wozunzika ndi wosauka,+

Ndipo usiku iye amakhala wakuba.+

15 Diso la wachigololo+ limadikira kuti mdima ugwe madzulo.+

Iye amati, ‘Palibe diso limene lindione,’+

Ndipo amaphimba kumaso kwake.

16 Mu mdima iye amathyola nyumba za anthu,

Masana iwo amadzitsekera m’nyumba,

Ndipo saona kuwala kwa masana.+

17 Kwa iwo m’mawa n’chimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,+

Chifukwa zoopsa zadzidzidzi za mu mdima wandiweyani amazidziwa.

18 Woipa amatengedwa mwamsanga ndi madzi.

Malo awo adzakhala otembereredwa padziko lapansi.+

Sadzapatukira kunjira yopita kuminda ya mpesa.

19 Chilala ndi kutentha zimatenga madzi a chipale chofewa.

Ndi mmenenso Manda amachitira ndi anthu amene achimwa.+

20 Mimba idzamuiwala, mphutsi zidzamumva kutsekemera pomuyamwa,+

Ndipo iye sadzakumbukiridwanso.+

Kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo.+

21 Woipa amachita zoipa ndi mkazi wouma amene sabereka,

Komanso ndi mkazi wamasiye+ amene woipayo sam’chitira zabwino.

22 Ndi mphamvu zake, Mulungu adzakoka anthu anyonga.

Oipa adzakhala apamwamba n’kumakayikira za moyo wawo.

23 Mulungu adzachititsa oipawo kuti azidzidalira+ n’cholinga choti azitha kudzisamalira.

Maso ake adzakhala panjira zawo.+

24 Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako n’kutha.+

Iwo amatsitsidwa,+ ndipo mofanana ndi wina aliyense amathotholedwa.

Amadulidwa mofanana ndi nsonga ya ngala za tirigu.

25 Choncho ndani amene anganene kuti ndine wabodza?

Kapena kunena kuti mawu anga ndi achabechabe?”

25 Tsopano Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:

 2 “Ulamuliro ndi wake ndipo iye ndi wochititsa mantha.+

Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.

 3 Kodi asilikali ake angatheke kuwawerenga?

Ndipo ndani amene kuwala kwake sikum’fika?

 4 Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?+

Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji woyera?+

 5 Kulitu mwezi koma si wowala.

Ndipo nyenyezi si zoyera m’maso mwake.

 6 Nanga kuli bwanji munthu yemwe ndi mphutsi,

Komanso mwana wa munthu yemwe ndi nyongolotsi?”+

26 Tsopano Yobu anayankha kuti:

 2 “Koma ndiyetu wathandiza munthu wopanda mphamvu!

Ukuona ngati wapulumutsa dzanja lopanda nyonga,+

 3 Walangiza munthu wopanda nzeru.+

Komanso ukuona ngati anthu ochuluka wawadziwitsa nzeru zopindulitsa.

 4 Kodi wauza ndani mawu ako,

Ndipo zimene ukunenazi zachokera kuti?

 5 Akufa amangokhalira kunjenjemera

Pansi pa nyanja ndi pansi pa zimene zili m’nyanjamo.+

 6 Manda ndi ovundukuka pamaso pake,+

Ndipo malo a chiwonongeko n’ngosavundikira.

 7 Iye anatambasula kumpoto pamwamba pa malo opanda kanthu,+

Ndipo anakoloweka dziko lapansi m’malere.

 8 Iye anakulunga madzi m’mitambo yake,+

Moti mitamboyo sing’ambika pansi pa madziwo.

 9 Anaphimba mpando wake wachifumu,

Poukuta ndi mtambo wake.+

10 Anaika malire ozungulira pamwamba pa madzi,+

Kumene kuwala kumakathera mu mdima.

11 Zipilala za kumwamba zimagwedezeka,

Ndipo zimadabwa chifukwa cha kudzudzula kwake.

12 Ndi mphamvu zake wavundula nyanja,+

Ndipo ndi kuzindikira kwake wathyolathyola+ wachiwawa.*+

13 Ndi mphepo yake wapukuta kumwamba,+

Ndipo dzanja lake labaya* njoka yokwawa.+

14 Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+

Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.

Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+

27 Tsopano Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo+ kuti:

 2 “Pali Mulungu wamoyo+ amene wandimana chilungamo,+

Ndiponso pali Wamphamvuyonse wamoyo amene wachititsa moyo wanga kupweteka,+

 3 Pamene mpweya wanga udakali wonse mwa ine,

Ndiponso pamene mzimu wa Mulungu udakali m’mphuno mwanga,+

 4 Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,

Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.

 5 Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama.+

Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.+

 6 Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya.+

Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.+

 7 Mdani wanga akhale munthu woipa m’zonse,+

Ndipo wondiukira akhaledi wochita zoipa.

 8 Kodi chiyembekezo cha wampatuko n’chiyani Mulungu akachotsa moyo wake,+

Akamulanda moyo wake?+

 9 Kodi Mulungu angamumvere kulira kwake

Zowawa zikamugwera?+

10 Kodi iye angasangalale ndi Wamphamvuyonse?

Kodi angapemphere kwa Mulungu nthawi zonse?

11 Ndikuphunzitsani ndi thandizo la Mulungu amuna inu.

Sindibisa maganizo a Wamphamvuyonse.+

12 Nonsenutu mwaona masomphenya.

Nanga n’chifukwa chiyani mukuoneka kuti ndinu opanda nzeru?+

13 Gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+

Zomwe adzalandire kwa Wamphamvuyonse monga cholowa cha ozunza anzawo, ndi izi:

14 Ana ake akachuluka, amachulukira lupanga.+

Mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira.

15 Opulumuka ake adzaikidwa m’manda pa nthawi ya mliri wakupha,

Ndipo akazi awo amasiye sadzalira.+

16 Iye akaunjika siliva ngati fumbi,

Ndipo akakonza zovala zake ngati dothi,

17 Ngakhale akonze zovalazo, wolungama ndi amene adzazivale.+

Ndipo silivayo, wosalakwa ndi amene adzam’tenge.

18 Iye wamanga nyumba yake ngati kadziwotche,

Ndiponso ngati chisimba*+ chimene mlonda wamanga.

19 Adzagona ali wolemera, koma palibe chimene chidzasonkhanitsidwe.

Adzatsegula maso ake, koma sipadzakhala kalikonse.+

20 Zoopsa zadzidzidzi zidzam’tenga ngati madzi.+

Usiku chimphepo chamkuntho chidzamuba ndithu.

21 Mphepo ya kum’mawa idzamunyamula n’kumusowetsa,+

Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+

22 Idzamukuntha, ndipo sidzamumvera chisoni.+

Adzayesera kuthawa mphamvu ya mphepoyo koma sadzatha.+

23 Anthu adzamuwombera m’manja monyoza.+

Ndipo adzamuimbira mluzu+ ali pamalo pake.

28 “Zoonadi, siliva ali ndi malo amene amapezekako,

Ndiponso kuli malo a golide yemwe amayengedwa.+

 2 Chitsulo chimatengedwa m’fumbi,+

Ndipo mkuwa umakhuthulidwa kuchokera m’miyala.

 3 Anthu aika malire a mdima,

Ndipo amafufuza miyala mpaka pamapeto,+

Mu mdima wandiweyani.

 4 Amakumba mgodi kutali ndi kumene anthu amakhala monga alendo,+

Kumalo oiwalika, kutali ndi phazi.

Anthu ena amatsikira pansi n’kumagwira ntchito cholendewera.

 5 Padziko lapansi pamamera chakudya,+

Koma pansi pake pasandulizidwa ngati kuti pasakazidwa ndi moto.

 6 M’miyala yake mumapezeka miyala ya safiro,+

Ndipo dzikolo lili ndi fumbi la golide.

 7 Imeneyi ndi njira imene mbalame yodya nyama+ sikuidziwa,

Ndipo diso la mphamba+ silinaionepo.

 8 Zilombo zamphamvu zakutchire sizinapondepondemo,

Mkango wamphamvu sunayendeyendemo.

 9 Anthu amatenga mwala wolimba,

Amagwetsa mapiri kuyambira pansi penipeni.

10 M’miyala amakumbamo ngalande zodzaza ndi madzi,+

Ndipo maso awo aona zinthu zonse zamtengo wapatali.

11 Kumalo kumene kumayambira mitsinje, amakumbako madamu.+

Ndipo chinthu chobisika amachibweretsa poyera.

12 Koma kodi nzeru zingapezeke kuti?+

Ndipo kumvetsa zinthu, malo ake ali kuti?

13 Munthu sadziwa mtengo wake,+

Ndipo nzeru sizipezeka m’dziko la amoyo.

14 Madzi akuya anena kuti,

‘Sizili mwa ine.’

Nayonso nyanja yanena kuti, ‘Sizili ndi ine.’+

15 Golide woyenga bwino sangaperekedwe mosinthana nazo,+

Ndipo sangayeze siliva monga mtengo wake.

16 Sangazigule ndi golide wa ku Ofiri,+

Kapena mwala wosowa wa onekisi ndi wa safiro.

17 Golide ndi galasi sizingayerekezedwe ndi nzeru,

Ndipo sangazisinthanitse ndi chiwiya chilichonse cha golide woyengeka bwino.

18 Mwala wamtengo wapatali wa korali+ ndi wa kulusitalo sizingayerekezedwe n’komwe ndi nzeruzo.

Ndipo thumba lodzaza ndi nzeru ndi lamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ndi ngale.+

19 Sizingayerekezedwe ndi miyala ya topazi+ ya ku Kusi,

Ngakhale golide woyenga bwino sangagulire nzeru.

20 Koma kodi nzeru zimachokera kuti?+

Ndipo kumvetsa zinthu malo ake ali kuti?

21 Zabisika ngakhale kumaso kwa munthu aliyense wamoyo,+

Ndipo n’zobisika kwa zolengedwa zouluka m’mlengalenga.

22 Chiwonongeko ndi imfa zanena kuti,

‘Ndi makutu athu, tamva nkhani zokhudza nzeruzo.’

23 Mulungu ndi amene amamvetsa njira zake,+

Ndipo iye ndiye amadziwa malo ake.

24 Pakuti iye amayang’ana kumapeto kwenikweni kwa dziko lapansi.+

Amaona pansi ponse pa thambo,

25 Kuti mphepo aipatse mphamvu.+

Ndipo iye amagawa madzi ndi choyezera.+

26 Pamene ankapangira mvula lamulo,+

Ndiponso pamene ankapangira njira mtambo wa mvula ya mabingu,

27 M’pamene anaona nzeru n’kuyamba kulankhula zinthu zokhudza nzeruzo.

Iye anazikonza n’kuzifufuza bwinobwino.

28 Ndiyeno anauza munthu kuti,

‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+

Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+

29 Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo kuti:

 2 “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili m’miyezi yakale,+

Ngati mmene ndinalili m’masiku amene Mulungu anali kundiyang’anira,+

 3 Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,

Pamene ndinkayenda mu mdima iye akundiunikira ndi kuwala kwake.+

 4 Ngati mmene ndinalili m’masiku amene ndinali mnyamata,+

Pamene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima, ndipo anali pahema wanga,+

 5 Pamene Wamphamvuyonse anali nane,

Pamene antchito anga onse anandizungulira,

 6 Pamene ndinkasambitsa mapazi anga m’mafuta a mkaka,

Ndiponso pamene miyala inkanditulutsira mitsinje ya mafuta.+

 7 Ndikapita kuchipata cha mzinda,+

Ndinkakonzako malo anga okhala pabwalo la mzinda.+

 8 Anyamata akandiona, ankabisala.

Ngakhale okalamba ankanyamuka n’kuima chilili.+

 9 Akalonga ankabweza mawu,

Ndipo ankagwira pakamwa.+

10 Mawu a atsogoleri ankabisika,

Ndipo lilime lawo linkamamatira m’kamwa mwawo.+

11 Khutu likamva, linkanena kuti ndine wodala,

Ndipo diso likaona, linkandichitira umboni.

12 Pakuti ndinkapulumutsa wosautsika wopempha thandizo,+

Ndiponso mwana wamasiye* ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+

13 Madalitso+ a munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa ankabwera kwa ine,

Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+

14 Ndinkavala chilungamo, ndipo icho chinkandiveka.+

Chilungamo changa chinali ngati malaya akunja odula manja, ndi nduwira.*

15 Ndinali ngati maso kwa wakhungu,+

Ndipo ndinali mapazi kwa wolumala.

16 Ndinali bambo weniweni kwa osauka,+

Ndipo mlandu wa munthu amene sindinali kumudziwa ndinkaufufuza.+

17 Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+

Ndipo wogwidwa, ndinkamulanditsa kukamwa kwa wochita zoipayo.

18 Ndinkati, ‘Ndidzafera m’chisa changa,+

Ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.+

19 Muzu wanga ndi wotseguka kuti uyamwe madzi,+

Ndipo mame akhala usiku wonse panthambi yanga.

20 Ulemerero wanga ndili nawobe,

Ndipo uta umene uli m’manja mwanga uziponya mivi mobwerezabwereza.’

21 Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira.

Ankakhala phee kuti amve malangizo anga.+

22 Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso.

Ndipo mawu anga ankadonthera pa iwo.+

23 Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,+

Ndipo ankayasama kuti m’kamwa mwawo mugwere mvula yomalizira.+

24 Ndinkawamwetulira, koma iwo sankakhulupirira,

Ndipo kuwala kwa pankhope+ panga sankakuzimitsa.

25 Ndinkawasankhira njira, ndipo ndinkakhala pansi patsogolo pawo.

Ndinali ngati mfumu pakati pa asilikali ake,+

Ndiponso ngati wotonthoza olira.+

30 “Tsopano anthu amene ndi ana aang’ono poyerekeza ndi ine,+

Akundiseka.+

Anthu amene abambo awo sindikanalola

Kuwaika pamodzi ndi agalu oweta nkhosa zanga.

 2 Ngakhale mphamvu za manja awo zinali zopanda ntchito kwa ine.

Ndiponso nyonga zawo zatha.+

 3 Chifukwa cha njala ndiponso kusowa, iwo ali ngati akufa.

Amatafuna dera lopanda madzi,+

Limene dzulo kunali mphepo yamkuntho ndi chiwonongeko.

 4 Iwo anali kubudula chitsamba cha mchere m’tchire,

Ndipo mizu ya timitengo ndiyo inali chakudya chawo.

 5 Ankathamangitsidwa m’mudzi.+

Anthu ankawakuwiza ngati mbala.

 6 Iwo amakhala m’malo otsetsereka a m’zigwa,*

M’maenje a m’nthaka ndi m’matanthwe.

 7 Amalira mokuwa ali pakati pa zitsamba,

Amaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.

 8 Ana a munthu wopusa,+ komanso ana a munthu wopanda dzina.

Iwo akwapulidwa n’kuthamangitsidwa m’dziko.

 9 Tsopano ine ndakhala mutu wa nyimbo yawo,+

Ndipo kwa iwo ndine chinthu choseketsa.+

10 Akunyansidwa nane, ndipo akukhala patali ndi ine.+

Sakuzengereza kundilavulira kumaso.+

11 Pakuti iye anakhwefula chingwe cha uta wanga n’kunditsitsa,

Ndipo zingwe za pakamwa pa hatchi,* iwo anazisiya zomasula chifukwa cha ine.

12 Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati kagulu ka anthu oipa.

Amasula mapazi anga,

Koma andiikira zopinga zovulaza kwambiri.+

13 Iwo awononga njira zanga.

Anangondibweretsera mavuto,+

Popanda aliyense wowathandiza.

14 Amabwera ngati akudutsa pampata waukulu,

Amakokoloka ndi madzi a mvula yamkuntho.

15 Zoopsa zadzidzidzi zandibwerera.

Ulemerero wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo,

Ndipo chipulumutso changa chapita ngati mtambo.

16 Tsopano moyo wanga ukukhuthuka mwa ine.+

Masiku a masautso+ ali pa ine.

17 Usiku mafupa anga+ amabooledwa n’kugwa pansi.

Zowawa zonditafuna sizipuma.+

18 Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu, chovala* changa chimasintha,

Ndipo chimandithina ngati kolala yothina.

19 Iye wanditsitsa mpaka m’dothi,

Moti ndikukhala ngati fumbi ndi phulusa.

20 Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha.+

Choncho ndaimirira kuti mundimvere.

21 Mwasintha n’kukhala wankhanza kwa ine.+

Ndi mphamvu yonse ya dzanja lanu, mwandisungira chidani.

22 Mwandiuluza ndi mphepo, mwandinyamula nayo.

Kenako mwandisungunula ndi mkokomo wake.

23 Pakuti ndikudziwa bwino kuti mudzandibwezera ku imfa,+

Kunyumba yosonkhanako aliyense wamoyo.

24 Koma palibe amene amatambasula dzanja lake polimbana ndi mulu wa zinthu zowonongeka.+

Komanso pa kuwonongeka kwa munthu, palibe amene amapempha thandizo la zinthu zimenezo.

25 Ndithu, ndalirira munthu amene zinthu sizikumuyendera bwino.+

Moyo wanga walirira munthu wosauka.+

26 Ngakhale kuti ndinkadikirira zabwino, zoipa n’zimene zinabwera.+

Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima.

27 Matumbo anga anawira ndipo sanakhale chete.

Masiku a masautso anandipeza.

28 Ndinayendayenda mwachisoni+ pamene kunalibe kuwala.

Ndinaimirira mumpingo, ndipo ndinkangofuula popempha thandizo.

29 Ndinakhala m’bale wake wa mimbulu,

Ndi mnzawo wa ana aakazi a nthiwatiwa.+

30 Khungu langa linakhala lakuda+ ndipo linayoyoka pathupi panga.

Mafupa anga anatentha chifukwa chouma.

31 Zeze wanga anangokhala wolirirapo,

Ndipo chitoliro changa chinangokhala choimbapo mawu a anthu olira.

31 “Ndachita pangano ndi maso anga.+

Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?+

 2 Kodi pali gawo lanji lochokera kwa Mulungu+ kumwamba,

Kapena cholowa chochokera kwa Wamphamvuyonse m’mwamba?

 3 Kodi si paja wochita zoipa amakumana ndi zosautsa,+

Ndipo ochitira anzawo zopweteka tsoka limawagwera?

 4 Kodi iye saona njira zanga,+

Ndi kuwerenga masitepe anga onse?

 5 Ngati ndayenda ndi anthu osanena zoona,+

Ndipo phazi langa lathamangira ku chinyengo,+

 6 Iye adzandiyeza pasikelo zolondola,+

Ndipo Mulungu adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.+

 7 Ngati ndaponda kumbali kusiya njira,+

Kapena ngati mtima wanga ukungotsatira maso anga,+

Kapenanso ngati cholakwa chilichonse chamatirira m’manja mwanga,+

 8 Ine ndibzale mbewu wina n’kudya,+

Ndipo mbadwa zanga zichotsedwe padziko.

 9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,+

Ndipo ndinali kudikirira+ pakhomo lolowera kunyumba kwa mnzanga,

10 Mkazi wanga aperere ufa mwamuna wina,

Ndipo amuna ena agone naye.+

11 Chifukwa limenelo lingakhale khalidwe lotayirira,

Ndipo chimenecho chingakhale cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza.+

12 Pakuti umenewu ndi moto umene unganyeketse zinthu mpaka kuziwononga,+

Ndipo unganyeketse mbewu zanga zonse ndi mizu yomwe.

13 Ngati ndinkalepheretsa chiweruzo cha kapolo wanga wamwamuna,

Kapena cha kapolo wanga wamkazi pa mlandu ndi ine,

14 Ndiye ndingatani Mulungu akaimirira,

Ndipo akandifunsa ndingamuyankhe chiyani?+

15 Kodi amene anandipanga m’mimba si amene anapanganso iyeyo?+

Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe m’mimba?

16 Ngati ndinkakaniza anthu onyozeka zopempha zawo,+

Ndipo ngati ndinkachititsa chisoni maso a mkazi wamasiye,+

17 Ngati ndinkanyema chakudya changa n’kumadya ndekha,

Mwana wamasiye* osadya nawo,+

18 (Pakuti kuyambira ubwana wanga iye wakula ndi ine ngati bambo ake,

Ndipo kuyambira m’mimba mwa mayi anga ndakhala ndikutsogolera mkazi wamasiyeyo).

19 Ngati ndinkaona munthu akuzunzika chifukwa chosowa chovala,+

Kapena kuona kuti wosauka alibe chofunda,

20 Ngati iye* sanandidalitse,+

Ndipo ngati sanavale ubweya+ wometedwa ku nkhosa zanga zamphongo zazing’ono kuti afundidwe,

21 Ngati ndili pachipata ndinaonapo mwana wamasiye akufunika thandizo langa,+

Koma ine n’kumuopseza ndi dzanja langa,+

22 Fupa la paphewa langa ligwe kuchoka m’malo mwake,

Ndipo fupa lakumtunda la dzanja langa lithyoke.

23 Chifukwa ine ndinkaopa tsoka lochokera kwa Mulungu,

Ndipo ulemu wake+ sindikanatha kulimbana nawo.

24 Ngati ndayesa golide chinthu chodalira,

Kapena ngati ndanena kwa golide kuti, ‘Ndimadalira iwe,’+

25 Ngati ndinkasangalala chifukwa chakuti ndinali ndi katundu wambiri,+

Ndiponso chifukwa chakuti dzanja langa linapeza zinthu zambiri,+

26 Ngati ndinkaona kuwala kukamanyezimira,

Kapena mwezi wamtengo wapatali ukuyenda,+

27 Ndipo mtima wanga unayamba kukopeka mobisa,+

Komanso dzanja langa linapsompsona pakamwa panga,

28 Chimenechonso chikanakhala cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza,

Chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba.

29 Ngati ndinkasangalala ndi kutha kwa munthu amene ankadana nane kwambiri,+

Kapena ngati ndinkakondwera chifukwa chakuti zoipa zam’gwera . . .

30 Ine sindinalole m’kamwa mwanga kuchimwa,

Popempha lumbiro loipira moyo wake.+

31 Ngati amuna a m’hema wanga sananene kuti,

‘Ndani angabwere ndi munthu amene sanakhute chakudya cha iye?’+ . . .

32 Palibe mlendo amene ankagona panja usiku.+

Zitseko zanga ndinkazisiya zotsegula kwa odutsa m’njira.

33 Ngati ndinabisa zolakwa zanga monga munthu wochokera kufumbi,+

Pobisa machimo anga m’thumba la malaya . . .

34 Chifukwa choopa khamu lalikulu,

Ndiponso chifukwa choopa kunyozedwa ndi mabanja,

Ndinkakhala chete, sindinkatuluka pakhomo.

35 Ndikulakalaka ndikanakhala ndi wina wondimvetsera,+

Kuti mogwirizana ndi chizindikiro changa chochita kulemba, Wamphamvuyonse andiyankhe.+

Ndikulakalaka munthu amene ali nane pa mlandu akanalemba chikalata.

36 Ndithu ndikanachinyamula paphewa.

Ndikanachizunguliza kumutu kwanga ngati chisoti chachikulu chachifumu.

37 Sindikanazengereza kumuuza za mayendedwe anga onse.+

Ndikanapita kwa iye ngati kwa mtsogoleri.

38 Ngati nthaka yanga ikanandilirira popempha thandizo,

Ndipo ngati mizere yake ikanalirira pamodzi,

39 Ngati ndadya zipatso zake osapereka ndalama,+

Ndipo ndachititsa moyo wa olima ake kupumira m’mwamba,+

40 M’malo mwa tirigu, pamere chitsamba chaminga,+

Ndipo m’malo mwa balere, pamere zitsamba zonunkha.”

Mawu a Yobu athera pamenepa.

32 Choncho amuna atatuwa anasiya kumuyankha Yobu, chifukwa iye anali kudziona kuti ndi wolungama.+ 2 Koma Elihu mwana wa Barakeli mbadwa ya Buza+ wa m’banja la Ramu anakwiya kwambiri. Anakwiyira Yobu chifukwa Yobuyo ankanena kuti anali wolungama, osati Mulungu.+ 3 Iye anakwiyiranso anzake atatu aja chifukwa chakuti iwo sanapeze yankho koma ankanena kuti Mulungu ndi woipa.+ 4 Elihu anali ndi mawu koma anadikira kuti Yobu amalize, chifukwa anthuwo anali aakulu kwa Elihuyo.+ 5 M’kupita kwa nthawi, Elihu anaona kuti amuna atatuwo analibe choyankha+ ndipo mkwiyo wake unakulirakulira. 6 Kenako Elihu mwana wa Barakeli mbadwa ya Buza anati:

“Ine ndine wamng’ono

Ndipo amuna inu ndinu achikulire.+

N’chifukwa chake ndinabweza mawu anga ndipo ndinaopa

Kukuuzani zimene ndikudziwa.

 7 Choncho ndinati, ‘Masiku alankhule.

Zaka zambiri n’zimene ziyenera kudziwitsa anthu nzeru.’+

 8 Ndithudi, mzimu wa anthu

Ndiponso mpweya wa Wamphamvuyonse n’zimene zimawachititsa kumvetsa zinthu.+

 9 Si anthu a masiku ambiri okha amene amakhala ndi nzeru,+

Ndipo si okalamba okha amene amadziwa kuweruza.+

10 Chotero ndinati, ‘Ndimvereni.

Ndikufuna kunena zimene ndikudziwa.’

11 Inetu ndimadikira kuti inu mulankhule.

Ndakhala ndikumvetsera maganizo anu,+

Kufikira mutapeza mawu oti munene.

12 Ndakhala ndikukumvetserani mwachidwi,

Ndipo palibe aliyense amene akum’dzudzula Yobu.

Palibe aliyense wa inu amene akuyankha zonena zake,

13 Kuti musanene kuti, ‘Tapeza nzeru.+

Mulungu ndiye akumuthamangitsa, osati munthu.’

14 Popeza sanalankhule mawu ondinena,

Ine sindimuyankha ndi mawu anu.

15 Iwo achita mantha, sakuyankhanso.

Mawu awathera.

16 Ine ndadikira, chifukwa sakupitiriza kulankhula.

Pakuti anangoima chilili, sanayankhenso.

17 Ine ndifotokozapo maganizo anga.

Ndinena zimene ndikudziwa,

18 Chifukwa ndili ndi mawu ambiri.

Mzimu wandikanikiza+ m’mimba mwanga.

19 Mimba yanga ili ngati vinyo amene alibe potulukira,

Ngati matumba atsopano, ikufuna kuphulika.+

20 Ndiloleni ndilankhule kuti ndipeze mpumulo.

Nditsegula pakamwa panga kuti ndiyankhe.+

21 Sindikondera munthu,+

Ndipo sindipereka dzina laulemu kwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+

22 Chifukwa sindikudziwa kuti ndingapereke bwanji dzina laulemu kwa munthu.

Pakuti amene anandipanga+ angandichotse mosavuta.

33 “Tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga,

Ndipo tcherani khutu ku zonena zanga zonse.

 2 Inetu nditsegula pakamwa panga,

Lilime langa ndi m’kamwa mwanga+ mulankhula.

 3 Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga,+

Ndipo milomo yanga imanena nzeru moona mtima.+

 4 Mzimu wa Mulungu unandiumba,+

Mpweya wa Wamphamvuyonse unandipatsa moyo.+

 5 Ngati mungathe ndiyankheni.

Ndifotokozereni mawu anu, ndipo khalani pamalo anu.

 6 Kwa Mulungu woona, ine ndili ngati inu nomwe.+

Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.+

 7 Mwa ine mulibe chinthu choti muope,

Ndipo mawu anga sakulemetsani.+

 8 Komabe inu mwanena m’makutu anga,

Ndipo ine ndakhala ndikumva mawu anu akuti,

 9 ‘Ndine woyera, wopanda tchimo,+

Ndilibe chondidetsa, ndilibe cholakwa.+

10 Mulungu amapeza ponditsutsira,

Amanditenga ngati mdani wake.+

11 Amaika mapazi anga m’matangadza,+

Amayang’anitsitsa njira zanga zonse.’+

12 Ndikukuuzani, pamenepa simunalondole.+

Chifukwa Mulungu ndi woposa kwambiri munthu.+

13 N’chifukwa chiyani mumalimbana naye?+

Kodi n’chifukwa chakuti sanakuyankheni mawu anu onse?+

14 Pakuti Mulungu amalankhula koyamba,

Kenako kachiwiri,+ ngakhale anthu asamvere.

15 Iye amawalankhula m’maloto+ ndi m’masomphenya+ a usiku,

Anthu akakhala m’tulo tofa nato,

Akamagona pabedi.+

16 Pa nthawi imeneyi m’pamene amatsegula anthu makutu,+

Pa chilimbikitso chake kwa iwo, amadindapo chidindo,

17 Kuti achotse munthu pa zochita zake,+

Ndi kuti mwamuna wamphamvu am’bisire kunyada.+

18 Amabweza munthu kuti asapite kudzenje,+

Ndiponso kuti moyo wake usaphedwe ndi chida.+

19 Kuwawa kumam’dzudzula iye ali pabedi pake,

Mafupa ake amangokhalira kukangana.

20 Moyo wake umanyansitsa chakudya,+

Ndipo iye amanyansidwa ndi chakudya chokoma.

21 Mnofu wake umatha, osaonekanso.

Mafupa ake amene sanali kuoneka amakhala pamtunda.

22 Iye amayandikira kudzenje,+

Ndipo moyo wake umayandikira kwa akupha.

23 Ngati iye ali ndi mthenga,

Womulankhulira mmodzi pa omulankhulira 1,000,

Kuti auze munthu zimene zili zowongoka,

24 Mulungu amasangalatsidwa naye ndi kunena kuti,

‘M’pulumutseni kuti asapite m’dzenje,+

Chifukwa ndapeza dipo.*+

25 Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata.+

Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.’+

26 Adzadandaulira Mulungu kuti asangalale naye,+

Adzaona nkhope yake akufuula mosangalala,

Ndipo Mulungu adzabwezera kwa munthu kulungama kwa Mulunguyo.

27 Adzaimbira anthu n’kunena kuti,

‘Ndachimwa,+ ndakhotetsa zimene zinali zowongoka,

Ndipo sindinayenere kuchita zimenezi.

28 Iye wandiwombola kuti ndisapite kudzenje,+

Ndipo moyo wanga udzaona kuwala.’

29 Mulungutu amachita zinthu zonsezi.

Kawiri kapena katatu konse, amachitira zimenezi mwamuna wamphamvu,

30 Kum’bweza kuti asapite kudzenje,+

Kuti aunikiridwe ndi kuwala kwa anthu amene ali moyo.+

31 Tcherani khutu inu a Yobu. Ndimvereni!

Khalani chete, ndipo ine ndipitiriza kulankhula.

32 Ngati muli ndi mawu, ndiyankheni.

Lankhulani chifukwa ine ndakondwera ndi kulungama kwanu.

33 Ngati mulibe mawu alionse, mvetserani mawu anga.+

Khalani chete, ndipo ine ndikuuzani nzeru.”

34 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:

 2 “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.

Ndipo anthu odziwa zinthu inu, ndimvereni.

 3 Pakuti khutu limasiyanitsa mawu,+

Monga mmene m’kamwa mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya.+

 4 Tiyeni tidzisankhire chiweruzo.

Tidziwe tokha pakati pathu chimene chili chabwino.

 5 Pakuti Yobu wanena kuti, ‘Ndithu ine si ine wolakwa,+

Koma Mulungu wapotoza chiweruzo changa.+

 6 Kodi ndikunama za mmene chiweruzo changa chiyenera kukhalira?

Chilonda changa chachikulu sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+

 7 Kodi ndi mwamuna wamphamvu uti amene ali ngati Yobu,+

Yemwe amamwa mnyozo ngati madzi?+

 8 Iye ndithu ali pa ulendo wokachita ubwenzi ndi anthu ochita zopweteka ena,

Komanso ali pa ulendo wokayenda ndi anthu oipa.+

 9 Chifukwa wanena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu sapindula kanthu+

Akamachita zosangalatsa Mulungu.’

10 Choncho inu amuna a mtima+ womvetsa zinthu, ndimvereni.

Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe,+

Ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.+

11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+

Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.

12 Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+

Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+

13 Ndani wam’patsa dziko lapansi?

Ndipo ndani wam’patsa ulamuliro panthaka yonse?

14 Akaika mtima wake pa munthu aliyense,

Akatenga mzimu* ndi mpweya wa munthuyo,+

15 Zamoyo zonse zimafera limodzi,

Ndipo munthu amabwerera kufumbi.+

16 Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi.

Mvetserani mawu anga.

17 Kodi zoonadi munthu wodana ndi chilungamo angalamulire?+

Ngati munthu wamphamvu ali wolungama, kodi munganene kuti ndi woipa?+

18 Kodi munthu anganene kwa mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake’?

Kapena angauze anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipa’?+

19 Alipo amene sanakonderepo akalonga,

Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+

Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+

20 Iwo amafa mwadzidzidzi,+ ngakhale pakati pa usiku.+

Anthuwo amagwedezeka uku ndi uku n’kufa,

Ndipo amphamvu amachoka popanda dzanja lowachotsa.+

21 Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+

Ndipo amaona mayendedwe ake onse.

22 Kulibe mdima wandiweyani

Woti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.+

23 Pakuti iye saikiratu nthawi yoti munthu aliyense

Apite kukaweruzidwa ndi Mulungu.

24 Iye amaphwanya amphamvu+ popanda kuwafufuza,

Ndipo amachititsa ena kuima m’malo mwawo.+

25 Chotero iye amazindikira ntchito zawo.+

Amawagwetsa usiku ndipo iwo amatswanyidwa.+

26 Amawamenya monga oipa,

Pamalo pomwe ena akuonerera.+

27 Chifukwa asiya kumutsatira,+

Ndipo sasamala za njira zake zonse,+

28 Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.

Choncho iye amamva kulira kwa osautsika.+

29 Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?

Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?

Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi.

30 Kuti munthu wopanduka asalamulire,+

Ndi kuti pasakhale misampha+ ya anthu.

31 Kodi munthu ndithu anganene kwa Mulungu kuti,

‘Ndapirira ngakhale kuti sindinachite cholakwa?+

32 Ngakhale kuti sindikuona chilichonse, inuyo ndiphunzitseni?

Ngati ndachita chosalungama chilichonse,

Sindidzachichitanso?’+

33 Kodi iye angakulipire mogwirizana ndi mmene ukuganizira, chifukwa chakuti ukukana chiweruzo chake?

Chifukwa chakuti iweyo wasankha wekha, osati ine?

Tsopano nena zimene ukudziwa.

34 Anthu a mtima womvetsa zinthu+ adzandiuza,

Ngakhale munthu wanzeru komanso wamphamvu amene akundimvetsera adzandiuza kuti,

35 ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+

Ndipo amanena mawu osonyeza kuti iye ndi wosazindikira.’

36 Atate anga, Yobu ayesedwe mpaka pamapeto

Chifukwa cha zimene anali kuyankha pakati pa amuna ochita zopweteka anzawo.+

37 Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+

Akuwomba m’manja pakati pathu ndipo akuchulutsa zonena zake zotsutsana ndi Mulungu woona.”+

35 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:

 2 “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo?

Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’+

 3 Mwanena kuti, ‘Kodi kulungamako n’kwantchito yanji kwa inu?+

Kodi kundipindulitsa chiyani kuposa chimene ndikanapindula pochimwa?’+

 4 Ineyo ndikuyankhani inuyo

Ndi mabwenzi+ anu muli nawowo.

 5 Yang’anani kumwamba+ muone.

Muona kuti mitambo+ ili pamwamba kuposa inu.

 6 Mukachimwa, kodi mumapindula chiyani chotsutsana naye?+

Ndipo kupanduka kwanu kukawonjezeka, kodi mumam’chitira chiyani chomuipira?

 7 Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani?

Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?+

 8 Kuipa kwanu kungapweteke munthu ngati inu nomwe,+

Ndipo chilungamo chanu chingakomere mwana wa munthu wochokera kufumbi.+

 9 Chifukwa cha kuchuluka kwa kuponderezedwa, iwo amangokhalira kufuula popempha thandizo.+

Amangokhalira kulirira thandizo chifukwa cha dzanja la amphamvu.+

10 Koma palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu,+ ali kuti,

Amene amapatsa anthu nyimbo usiku?’+

11 Iye ndiye amatiphunzitsa+ zambiri kuposa nyama zakutchire,+

Ndipo amatipatsa nzeru kuposa ngakhale zolengedwa zouluka m’mlengalenga.

12 Iwo amangokhalira kulirira thandizo, koma iye sawayankha+

Chifukwa cha kunyada+ kwa anthu oipa.

13 Koma Mulungu samva kufuula kwa anthu olankhula zinthu zonama,+

Ndipo Wamphamvuyonse sawaona.+

14 Nanga kuli bwanji mukanena kuti simumuona?+

Mlanduwo uli pamaso pake, choncho muzimuyembekezera ndi nkhawa.+

15 Tsopano popeza sanakulangeni chifukwa cha mkwiyo wake,+

Iye sanaonenso kupupuluma kwanu.+

16 Yobu akatsegula pakamwa pake amalankhula zopanda pake.

Amachulukitsa mawu osonyeza kuti palibe chimene akudziwa.”+

36 Elihu anapitiriza kunena kuti:

 2 “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa ndipo ndikuuzani

Kuti mawu alipobe oti ndinene m’malo mwa Mulungu.

 3 Zimene ndinene ndizitenga kutali,

Ndipo ndilengeza kuti amene anandipanga, ndiye mwiniwake wa chilungamo.+

 4 Chifukwa mawu anga ndithu si onama.

Wodziwa bwino zinthu kwambiri+ ali ndi inu.

 5 Mulungutu ndi wamphamvu+ ndipo sadzakana munthu.

Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.

 6 Iye sadzasiya woipa aliyense ali wamoyo,+

Koma adzapereka chiweruzo cholungama kwa osautsika.+

 7 Sadzachotsa maso ake pa aliyense wolungama.+

Adzaika mafumu pamipando yachifumu,+

Adzawachititsa kuti alamulire kwamuyaya, ndipo iwo adzakhala ndi mphamvu zambiri.

 8 Anthu akamangidwa m’matangadza,+

Amagwidwa ndi zingwe za masautso.

 9 Ndiyeno iye adzawauza za momwe iwo amachitira zinthu

Ndiponso zolakwa zawo, chifukwa iwo amadzikuza.

10 Iye adzatsegula makutu awo kuti iwo amve pamene iye akuwalimbikitsa,+

Ndipo adzawauza kuti asiye kuchita zopweteka ena.+

11 Akamumvera ndi kumutumikira,

Adzamaliza bwino masiku awo,

Ndipo adzamaliza zaka zawo mosangalala.+

12 Koma akapanda kumvera, adzaphedwa+ ndi chida.+

Iwo adzafa ali osadziwa.

13 Anthu ampatuko adzaunjika mkwiyo.+

Iwo sadzalirira thandizo chifukwa chakuti iye wawamanga.

14 Iwo adzafa ali anyamata,+

Ndipo moyo wawo udzathera pakati pa mahule aamuna a pakachisi.+

15 Iye adzapulumutsa wozunzika m’masautso ake,

Ndipo adzatsegula makutu awo pamene akuponderezedwa.

16 Ndithu iye adzakukopani n’kukuchotsani pakamwa pa zowawa.+

M’malomwake padzakhala malo otakasuka,+ osati opanikiza,

Ndipo chitonthozo cha patebulo panu chidzakhala chodzaza ndi mafuta.+

17 Ndithu mudzakhutira woipa+ akadzaweruzidwa.

Chiweruzo ndi chilungamo zidzakhazikika.

18 Samalani kuti mkwiyo+ usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru,

Ndipo dipo lalikulu+ lisakusocheretseni.

19 Kodi kulira kwanu kopempha thandizo kudzakupindulirani?+ Ayi, sikudzakupindulirani ngakhalenso pa mavuto,

Ngakhale muyesetse mwamphamvu bwanji.+

20 Musapumire m’mwamba polakalaka usiku,

Pamene anthu amabwera kuchokera kumene anali.

21 Samalani kuti musabwerere ku zinthu zopweteka ena,+

Chifukwa mwasankha zimenezi m’malo mwa masautso.+

22 Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake.

Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye?

23 Ndani wam’funsa kuti afotokoze za njira yake,+

Ndipo ndani wamuuza kuti, ‘Mwachita zosalungama’?+

24 Kumbukirani kuti muyenera kutamanda ntchito zake,+

Zimene anthu amaziimba.+

25 Anthu onse amaziyang’anitsitsa.

Munthu amaziyang’ana ali patali.+

26 Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.+

Zaka zake n’zosawerengeka.+

27 Pakuti iye amakoka madontho a madzi.+

Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu,

28 Moti mitambo imakha,+

Imakhetsa madzi ochuluka pa anthu.

29 Zoonadi, ndani angamvetse mmene mitambo imatambasukira?

Komanso kugunda kochokera kumsasa wake?+

30 Amaikuta ndi kuwala kwake,+

Ndipo waphimba mizu ya nyanja.

31 Ndi zimenezi, iye amaweruza mokomera mitundu ya anthu.+

Amapereka chakudya chochuluka.+

32 Iye wafumbata mphezi m’manja mwake,

Ndipo amailamula kuti igwere woukira.+

33 Kugunda kwake+ kumanena za iye.

Ziwetonso zimanena za amene akubwera.

37 “Chifukwa cha zimenezi, mtima wanga wayamba kunjenjemera,+

Ndipo ukudumpha kuchoka m’malo mwake.

 2 Amuna inu mvetserani mwatcheru kugunda kwa mawu a Mulungu,+

Ndi kubangula kochokera m’kamwa mwake.

 3 Amakuchititsa kumveka pansi ponse pa thambo,

Ndipo mphezi yake+ imafika kumalekezero a dziko lapansi.

 4 Pambuyo pake pamamveka phokoso.

Iye amabangula+ ndi mawu ake amphamvu.+

Mawu ake akamveka, iye saletsa mphezizo.+

 5 Mulungu amabangula ndi mawu ake+ mochititsa chidwi kwambiri.

Amachita zinthu zazikulu zimene sitingazidziwe.+

 6 Chifukwa chipale chofewa amachiuza kuti, ‘Gwera padziko lapansi.’+

Amauzanso mvula zimenezi, ngakhalenso mvula yamphamvu ikamakhuthuka.+

 7 Iye amatseka dzanja la munthu aliyense,

Kuti anthu onse adziwe ntchito ya Mulungu.

 8 Nyama yakutchire imapita kukabisala,

Ndipo imakhala m’malo ake obisala.+

 9 Mphepo yamkuntho imachokera m’chipinda chamkati,+

Ndipo kuzizira kumachokera mumphepo yakum’mawa.+

10 Mpweya wa Mulungu umapereka madzi oundana,+

Ndipo malo aakulu a madzi ndi oundana.+

11 Iye amalemetsa mitambo ndi chinyontho.

Kuwala kwake+ kumamwaza mitambo younjikana pamodzi.

12 Amaizunguliza ndi kuiwongolera kuti igwire ntchito yake

Kulikonse kumene amailamula+ panthaka ya padziko lapansi.

13 Amagwiritsa ntchito mitamboyo kuti ipereke chilango,+ kuti inyowetse dziko lake,+

Komanso kuti iye asonyeze kukoma mtima kwake kosatha.+

14 Mvetserani izi inu a Yobu:

Imani chilili ndi kuganizira mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.+

15 Kodi mukudziwa nthawi imene Mulungu anapangana nazo,+

Komanso pamene anachititsa kuunika kwa mtambo wake kuti kuwale?

16 Kodi mukudziwa mmene mtambo umaimira,+

Ndiponso ntchito zodabwitsa za yemwe amadziwa zinthu bwino kwambiri?+

17 Kodi mukudziwa momwe zovala zanu zimatenthera,

Dziko likakhala chete kuyambira kum’mwera?+

18 Kodi limodzi ndi iyeyo mungagangate* kuthambo,+

Komwe kuli ngati galasi lolimba lopangidwa ndi chitsulo chosungunula?

19 Tidziwitseni zoti timuuze.

Sitingathe kutulutsa mawu chifukwa cha mdima.

20 Kodi auzidwe kuti ndikufuna kulankhula?

Kapena kodi munthu wina wanena kuti mawu alankhulidwa?+

21 Tsopano iwo sakuona kuwala.

Kuthambo kumanyezimira,

Mphepo ikadutsa n’kuyeretsako.

22 Kunyezimira ngati kwa golide kumachokera kumpoto.

Ulemu+ wa Mulungu ndi wochititsa mantha.

23 Wamphamvuyonse sitikumudziwa.+

Iye ali ndi mphamvu zambiri,+

Ndipo sadzanyoza+ chilungamo+ ndi kulungama kochuluka.+

24 Choncho anthu amuope.+

Iye saganizira aliyense amene amadziona kuti ndi wanzeru.”+

38 Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:

 2 “Kodi amene akuphimba malangizo anga

Ndi mawu ake opanda nzeruyu ndani?+

 3 Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu.

Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+

 4 Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi?+

Ndiuze ngati uli womvetsa zinthu.

 5 Ndani anaika miyezo yake, ngati ukudziwa,

Kapena ndani anatambasulirapo chingwe choyezera?

 6 Kodi maziko ake anazikidwa pa chiyani?+

Kapena ndani anaika mwala wake wapakona,

 7 Pamene nyenyezi za m’mawa+ zinafuula pamodzi mokondwera,

Ndiponso pamene ana onse a Mulungu+ anayamba kufuula ndi chisangalalo?

 8 Ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+

Imene inayamba kuyenda ngati kuti ikutumphuka m’mimba?

 9 Pamene ndinaika mtambo ngati chovala chake,

Ndi mdima wandiweyani ngati nsalu yoikulungira.

10 Ndipo ndinaiikira lamulo,

Ndinaiikiranso mpiringidzo ndi zitseko.+

11 Kenako ndinaiuza kuti, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,+

Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepa.’+

12 Kodi kuyambira masiku ako oyambirira unalamula m’mawa?+

Kodi ndiwe unachititsa m’bandakucha kudziwa malo ake,

13 Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi,

Kuti anthu oipa asansidwe n’kuchotsedwamo?+

14 Dzikolo limadzisintha ngati dongo+ pansi pa chodindira,

Ndipo zinthu zimakhala pamalo awo ngati kuti zavala zovala.

15 Kuwala kwa oipa kumachotsedwa,+

Ndipo dzanja lokwezedwa m’mwamba limathyoledwa.+

16 Kodi unafika ku akasupe a nyanja,

Kapena kodi unayamba wakafunafunapo madzi akuya?+

17 Kodi anakuvundukulira zipata za imfa,+

Kapena zipata za mdima wandiweyani,+ kodi ungathe kuziona?

18 Kodi unaganizapo mozama za kukula kwa dziko lapansi?+

Ndiuze ngati ukudziwa zonse.

19 Kodi njira yopita kumene kuwala kumakhala ili kuti?+

Nanga mdima, kwawo n’kuti,

20 Kuti uzipititse kumalire awo,

Ndi kuti udziwe njira zopita kunyumba kwawo?

21 Kodi ukudziwa popeza pa nthawiyo unali utabadwa,+

Ndiponso chifukwa chakuti masiku ako ndi ochuluka?

22 Kodi unalowapo munkhokwe ya chipale chofewa,+

Kapena umaziona nkhokwe za matalala,+

23 Zimene ndazisungira nthawi ya zowawa,

Ndi tsiku lomenyana komanso lankhondo?+

24 Kodi njira imene kuwala kumadzigawira ili kuti,

Ndiponso njira imene mphepo ya kum’mawa+ imamwazikira padziko lapansi ili kuti?

25 Ndani anagawa ngalande ya madzi osefukira,

Ndi njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+

26 Kuti achititse mvula kugwa padziko pamene palibe munthu,+

Ndi kuchipululu kumene kulibe munthu aliyense,

27 Kuti inyowetse malo owonongeka ndi mvula yamkuntho ndiponso ouma,

Komanso kuti imeretse udzu?+

28 Kodi mvula ili ndi tate wake,+

Kapena ndani anabereka mame?+

29 Kodi madzi oundana amachokera m’mimba mwa ndani,

Ndipo mame oundana+ a m’mlengalenga anawabereka ndani?

30 Madzi amadzibisa ngati kuti ali pansi pa mwala,

Ndipo pamwamba pa madzi akuya pamauma.+

31 Kodi ungamange zingwe gulu la nyenyezi la Kima,

Kapena kodi ungamasule zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+

32 Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi la Mazaroti pa nthawi yake?

Ndipo kodi ungatsogolere gulu la nyenyezi la Asi pamodzi ndi ana ake?

33 Kodi malamulo akuthambo ukuwadziwa,+

Kapena kodi ulamuliro wake ungauike padziko lapansi?

34 Kodi ungafuulire mtambo

Kuti madzi ochuluka akukhuthukire?+

35 Kodi ungauze mphezi kuti zibwere kwa iwe

N’kudzakuuza kuti, ‘Ndife pano, tabwera’?

36 Ndani anaika nzeru+ m’mitambo,

Kapena zinthu zochitika kuthambo, ndani anazipatsa kuzindikira?+

37 Ndani amene ali ndi nzeru zoti angathe kudziwa chiwerengero cholondola cha mitambo,

Kapena zosungira madzi akumwamba, ndani angathe kuzipendeketsa,+

38 Fumbi likasanduka matope n’kumayenderera ngati chitsulo chosungunula,

Ndiponso zibuma zadothi zikamatana?

39 Kodi mkango ungausakire nyama,

Ndipo kodi ungakhutiritse mikango yamphamvu yanjala kwambiri,+

40 Ikamyata m’malo amene imabisala,+

Kapena ikabisala patchire kuti igwire nyama?

41 Ndani amakonzera khwangwala chakudya,+

Ana ake akamalirira Mulungu kuti awathandize,

Akamadzandira chifukwa chosowa chakudya?

39 “Kodi ukudziwa nthawi yoikidwiratu imene mbuzi za m’mapiri zokhala m’matanthwe zimabereka?+

Kodi unaona nthawi imene mphoyo zimabereka+ ndi zowawa za pobereka?

 2 Kodi umawerenga miyezi imene zimakwanitsa,

Kapena ukudziwa nthawi yoikidwiratu imene zimabereka?

 3 Zimagwada zikamaswa ana awo,

Ululu wawo ukamatha.

 4 Ana awo amakhala amphamvu ndi athanzi, ndipo amakulira m’tchire.

Amachoka osabwereranso kwa makolo awo.

 5 Ndani anapatsa mbidzi+ ufulu wongodziyendera,

Ndipo ndani anamasula zingwe za bulu wam’tchire,

 6 Amene ndinam’patsa chipululu monga nyumba yake,

Ndiponso amene amakhala kudera la nthaka yamchere?+

 7 Amaseka chipwirikiti cha m’mudzi.

Samva phokoso la wowenda nyama.+

 8 Amayendayenda m’mapiri pofunafuna msipu,+

Ndipo amafunafuna chomera chilichonse chobiriwira.+

 9 Kodi ng’ombe yamphongo yam’tchire* imafuna kukutumikira,+

Kapena ingagone pafupi ndi chodyeramo ziweto zako?

10 Kodi ungaimange zingwe kuti ilime mizere,

Kapena kodi ingasalaze+ zigwa pambuyo pako?

11 Kodi ungaikhulupirire chifukwa ili ndi mphamvu zochuluka,

Kapena ungaisiyire ntchito yako?

12 Kodi ungaidalire kuti ikubweretsere mbewu zako,

Ndi kuti izitutire popunthira?

13 Kodi nthiwatiwa yaikazi imakupiza mapiko ake mosangalala,

Kapena kodi ili ndi mapiko ndi nthenga zofanana ndi za dokowe?+

14 Pakuti imasiya mazira ake munthaka,

Ndipo imawatenthetsa m’fumbi.

15 Imaiwala kuti phazi linalake likhoza kuwaphwanya,

Kapenanso kuti nyama yakutchire ikhoza kuwaponda.

16 Imachitira nkhanza ana ake ngati kuti si ake,+

Ndipo imagwira ntchito pachabe chifukwa ilibe mantha.

17 Pakuti Mulungu waichititsa kuiwala nzeru,

Ndipo sanaigawireko kuzindikira.+

18 Ikatambasula mapiko ake ndi kuwakupiza,

Imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.

19 Kodi hatchi ungaipatse mphamvu?+

Kodi ungaveke khosi lake manyenje awirawira?

20 Kodi ungaichititse kudumpha ngati dzombe?

Ulemerero wa kumina kwake n’ngoopsa.+

21 Imachita mgugu+ m’chigwa, ndipo imadumpha mwamphamvu.

Imapita kukakumana ndi zida zankhondo.+

22 Imaseka zoopsa ndipo sichita mantha.+

Sibwerera ikaona lupanga.

23 Kachikwama koika mivi kamachita phokoso kakamagunda m’nthiti mwake

Limodzi ndi mkondo ndi nthungo.*

24 Imatha mtunda mwamgugu ndiponso mosangalala.

Ikamva kulira kwa lipenga sikhulupirira chifukwa cha chisangalalo.

25 Lipenga likangolira, imati eyaa!

Imanunkhiza nkhondo ili kutali,

Imamva phokoso la mafumu ndi mfuu yankhondo.+

26 Kodi kuzindikira kwako n’kumene kumachititsa kabawi kuuluka pamwamba,

Ndi kutambasulira mapiko ake mphepo yakum’mwera?

27 Kapena kodi lamulo lako n’limene limachititsa chiwombankhanga+ kuulukira m’mwamba,

Ndi kumanga chisa chake pamwamba kwambiri,+

28 Kukhala pathanthwe ndi kugona pomwepo usiku,

Pansonga penipeni pa thanthwe ndi pamalo povuta kufikapo?

29 Chimafunafuna chakudya kuchokera pamenepo.+

Maso ake amaona kutali kwambiri.

30 Ana ake amakhalira kumwa magazi.

Kumene kuli zakufa, icho chimakhala komweko.”+

40 Tsopano Yehova anafunsa Yobu kuti:

 2 “Kodi munthu ayenera kum’tola chifukwa Wamphamvuyonse, n’kutsutsana naye?+

Amene akudzudzula Mulungu ayankhe.”+

3 Ndiyeno Yobu anamuyankha Yehova kuti:

 4 “Ine tsopano ndakhala wopanda pake.+

Kodi ndingakuyankheni chiyani?

Ndaika dzanja langa pakamwa.+

 5 Ndalankhula kamodzi ndipo sindiyankhanso.

Sindionjezera chilichonse pa mawu amene ndalankhula kawiri.”

6 Tsopano Yehova anamuyankha Yobu kuchokera mumphepo yamkuntho+ kuti:

 7 “Takokera chovala chako n’kuchimanga m’chiuno ngati mwamuna wamphamvu.+

Ndikufuna ndikufunse mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+

 8 Kodi ndithu ukuchititsa chilungamo changa kukhala chopanda pake?

Kodi ukunena kuti ine ndine wolakwa kuti iweyo ukhale wolondola?+

 9 Kapena kodi uli ndi dzanja ngati la Mulungu woona?+

Kodi ungachititse mabingu kugunda ndi mawu ngati a Mulungu?+

10 Tadziveka ukulu+ ndiponso kukwezeka,+

Ndipo uvale ulemu+ ndi ulemerero.+

11 Mkwiyo wako wosefukira utuluke,+

Ndipo uone aliyense wodzikweza n’kumutsitsa.

12 Uone wodzikweza aliyense n’kumuchepetsa,+

Ndipo oipa uwaponderezere pamalo pomwe alilipo.

13 Uwabise pamodzi m’fumbi,+

Uphimbe nkhope zawo m’malo obisika,

14 Ndipo ineyo ndidzakuyamikira,

Chifukwa chakuti dzanja lako lamanja lingakupulumutse.

15 Ine ndinapanga mvuu* ndipo ndinapanganso iweyo.

Iyo imadya udzu wobiriwira+ ngati ng’ombe yamphongo.

16 Mphamvu zake zili m’chiuno mwake,

Ndipo minofu ya pamimba pake ndi yamphamvu kwambiri.+

17 Imapindira pansi mchira wake ngati mtengo wa mkungudza,

Mitsempha ya m’ntchafu mwake ndi yolukanalukana.

18 Mafupa ake ali ngati mapaipi amkuwa,

Mafupa ake olimba ali ngati ndodo zachitsulo.

19 Iyo ndiyo chiyambi cha njira za Mulungu.

Amene anaipanga+ akhoza kubweretsa pafupi lupanga lake.

20 Pakuti mapiri amaberekera iyoyo mbewu zawo,+

Ndipo nyama zonse zakutchire zimasewera pamenepo.

21 Imagona pansi pa mitengo yaminga,

Pamalo obisika m’mabango+ ndi m’madambo.+

22 Mitengo yaminga imaitchinga ndi mthunzi wawo.

Mitengo ya msondodzi ya kuchigwa* imazungulira mvuuyo.

23 Mtsinje ukakalipa iyo sichita mantha n’kuthawa.

Sitekeseka ngakhale madzi a mu Yorodano+ asefukire n’kumainyowetsa kumaso.

24 Kodi alipo amene angaigwire iyo ikuona?

Kodi alipo amene angakole mphuno yake ndi ngowe?

41 “Kodi ungawedze ng’ona*+ ndi mbedza?

Kapena ungamange lilime lake ndi chingwe?

 2 Kodi ungaike chingwe cha udzu* m’mphuno mwake?+

Kapena kodi ungaboole nsagwada zake ndi minga?

 3 Kodi iyo ingachonderere kambirimbiri kwa iwe,

Kapena kodi ingalankhule nawe mofatsa?

 4 Kodi ingachite nawe pangano,

Kuti uitenge ngati kapolo mpaka kalekale?

 5 Kodi ungasewere nayo ngati mbalame,

Kapena kodi ungaimange kuti izisangalatsa ana ako aakazi?

 6 Kodi ochita malonda angaigule posinthanitsa ndi chinthu china?

Kodi angaigawe pakati pa amalonda?

 7 Kodi ungadzaze khungu lake ndi ntcheto,*+

Kapena mutu wake ndi mikondo yophera nsomba?

 8 Ika dzanja lako pa iyo.

Kumbukira nkhondoyo. Usadzachitenso.

 9 Ndithu, zimene munthu anali kuyembekezera adzakhumudwa nazo,

Komanso adzagwa pansi akangoiona.

10 Palibe angalimbe mtima kuti aipute.

Kodi ndani angaimitsane nane?+

11 Ndani wayamba kundipatsa kanthu, kuti ndim’patse mphoto?+

Zinthu zonse za pansi pa thambo ndi zanga.+

12 Sindikhala chete osanena za ziwalo zake,

Kapena za mphamvu zake ndi kukongola kwa thupi lake loumbidwa bwino.

13 Ndani angaivule chovala chake?

Ndani angalowe pakati pa nsagwada zake?

14 Ndani watsegula zitseko za kumaso kwake?

Mano ake onse ndi ochititsa mantha.

15 Mizere ya mamba ake ndiyo kudzikuza kwake.

Iwo ndi otsekeka ngati anachita kuwamatirira pamodzi.

16 Ndi othithikana kwambiri,

Moti ngakhale mpweya sungadutse pakati pawo.

17 Onse anamatirirana.

Anagwirana ndipo sizingatheke kuwalekanitsa.

18 Ikamatulutsa mpweya, pamaoneka kuwala.

Maso ake ali ngati kuwala kwa m’bandakucha.

19 M’kamwa mwake mumatuluka kung’anima kwa mphezi,

Ngakhale moto wothetheka umatulukamo.

20 M’mphuno mwake mumatuluka utsi,

Ngati ng’anjo imene yayatsidwa ndi udzu.

21 Moyo wake umayatsa makala.

Ngakhale lawi la moto limatuluka m’kamwa mwake.

22 M’khosi mwake mumakhala mphamvu,

Ndipo pamaso pake, kutaya mtima kumadumpha.

23 Minofu yake yokwinyika imamatana.

Imakhala ngati anaiumbira pomwepo ndipo sisunthika.

24 Mtima wake anauumba kuti ukhale wolimba ngati mwala.

Anauumbadi ngati mwala wapansi wa mphero.

25 Ikadzuka, amphamvu amachita mantha.+

Ikathedwa nzeru, amadabwa kwambiri.

26 Lupanga silitha kuigonjetsa,

Ngakhalenso mkondo, mpaliro, kapena muvi.+

27 Chitsulo+ imangochiona ngati udzu,

Ndipo mkuwa imangouona ngati mtengo wowola.

28 Muvi suithamangitsa.

Miyala yoponya ndi gulaye*+ imasanduka mapesi kwa iyo.

29 Chibonga imangochiona ngati phesi.+

Imaseka ikamva phokoso la nthungo.

30 Kumimba kwake kuli ngati timapale tosongoka.

Imayala chopunthira mbewu+ pamatope.

31 Imachititsa madzi akuya kuwira ngati mphika.

Imachititsa nyanja kukhala ngati mphika wa mafuta onunkhira.

32 Imachititsa njira kuwala m’mbuyo mwake.

Munthu angaone madzi akuya ngati kuti ndi imvi.

33 Pafumbi palibe chofanana nayo.

Iyo inapangidwa kuti isamachite mantha.

34 Imaona chilichonse chokwezeka.

Iyo ndi mfumu ya zilombo zonse zakutchire.”

42 Tsopano Yobu anamuyankha Yehova kuti:

 2 “Ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse,+

Ndipo palibe zimene simungakwanitse.+

 3 Inu munati, ‘Kodi amene akuphimba malangizo anga mopanda nzeruyu ndani?’+

Chotero ine ndinalankhula, koma sindinali kuzindikira

Zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine, zimene sindikuzidziwa.+

 4 Inu munati, ‘Tamvera, ndikufuna ndikulankhule.

Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.’+

 5 Ndinkangomva za inu,

Koma tsopano diso langa lakuonani.

 6 N’chifukwa chake ndikubweza mawu anga,

Ndipo ndikulapa+ m’fumbi ndi m’phulusa.”

7 Yehova atanena mawu amenewa kwa Yobu, Yehovayo anauza Elifazi wa ku Temani kuti:

“Mkwiyo wanga wayakira iweyo ndi anzako awiriwo+ chifukwa inu simunanene zoona za ine,+ monga wachitira Yobu mtumiki wanga. 8 Tsopano utenge ng’ombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.+ Upite nazo kwa mtumiki wanga Yobu,+ ndipo inuyo mukadziperekere nsembe yopsereza. Ndiyeno Yobu mtumiki wanga akakupemphererani.+ Ine ndimvera iye yekhayo basi kuti ndisakuchititseni manyazi chifukwa cha zopusa zimene mwachita, popeza simunanene zoona za ine monga wachitira Yobu mtumiki wanga.”+

9 Chotero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Shuwa ndi Zofari wa ku Naama anapita n’kukachita monga mmene Yehova anawauzira. Choncho Yehova anamva pemphero la Yobu.

10 Tsopano Yehova anathetsa masautso a Yobu+ pamene iye anapempherera anzake aja.+ Kuwonjezera pamenepo Yehova anayamba kum’patsa Yobu zonse zimene anali nazo, kuwirikiza kawiri.+ 11 Abale ake onse, alongo ake onse ndi onse amene anali kumudziwa kale+ ankabwera kwa iye. Iwo anayamba kudyera naye pamodzi mkate+ m’nyumba mwake, komanso anali kumulimbikitsa ndi kum’pepesa chifukwa cha tsoka lonse limene Yehova analola kuti lim’gwere. Aliyense wa iwo anapatsa Yobu mphatso ya ndalama ndi mphete yagolide.

12 Yehova anadalitsa+ kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake+ moti iye anakhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ng’ombe 2,000 zimene zinkagwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 1,000. 13 Anakhalanso ndi ana aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.+ 14 Mwana wake wamkazi woyamba anam’patsa dzina lakuti Yemima, wachiwiri Keziya ndipo wachitatu Kereni-hapuki. 15 M’dziko lonselo munalibe akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, ndipo bambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi abale awo.+

16 Pambuyo pa zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140+ ndipo anaona ana ake ndi zidzukulu zake+ mpaka m’badwo wachinayi. 17 Pomalizira pake Yobu anamwalira ali wokalamba ndiponso wokhutira ndi masiku ake.+

Kapena kuti “mchimwene.”

M’Chiheberi, “Leviyatani.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti “amithenga.”

Mawu ake enieni, “woyera.”

Onani Mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Ena amati “manthova,” kapena “mambidza.”

Onani Zakumapeto 5.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “nyumba.”

Ena amati “nthota.”

Kutanthauza, “fano.”

Mawu ake enieni, “kunyamula mnofu wanga ndi mano.”

Kapena kuti “munthu uyu.” M’Chiheberi, “iye” kutanthauza “Yobu.”

Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.

Mawu ake enieni, “oyera.”

Ena amati “masaka.”

Mawu ake enieni, “Anzanga akungokhalira kuika usiku m’malo mwa masana.”

Mawu ake enieni, “ndapulumuka ndi khungu la mano anga.”

Mawu ake enieni, “amene maso anga adzamuonadi, koma osati mlendo.”

Ena amati “zimanzuna.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Mwina “wachiwawa” ameneyu ndi chilombo cha m’nyanja.

Ena amati “kulasa.”

Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”

N’kutheka kuti akutanthauza “khungu.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Mawu ake enieni, “chiuno chake.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto 4.

Ena amati “kutchaya,” kapena “kutsendera.”

Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.

Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.

M’Chiheberi, “Behemoti.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

M’Chiheberi, “Leviyatani.”

Mawu ake enieni, “mlulu.”

Umenewu ndi mpaliro umene mwina unali ndi mano oyang’ana kumbuyo ngati dzino la mbedza.

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena