Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Exodus 1:1-40:38
  • Ekisodo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ekisodo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Ekisodo

Ekisodo

1 Pamene Yakobo, kapena kuti Isiraeli anapita ku Iguputo, aliyense mwa ana ake aamuna anapitanso limodzi ndi banja lake. Mayina a ana a Yakobowo ndi awa:+ 2 Rubeni,+ Simiyoni,+ Levi,+ Yuda,+ 3 Isakara,+ Zebuloni,+ Benjamini,+ 4 Dani,+ Nafitali,+ Gadi+ ndi Aseri.+ 5 Yosefe anali kale ku Iguputo.+ Anthu onse otuluka m’chiuno mwa Yakobo+ analipo 70. 6 Patapita nthawi Yosefe anamwalira.+ Ndipo abale ake onse ndi m’badwo wonsewo anamwaliranso. 7 Ana a Isiraeli anaberekana ndipo anachuluka m’dzikomo. Iwo anapitiriza kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa, moti anadzaza m’dzikomo.+

8 Patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinam’dziwe Yosefe inayamba kulamulira mu Iguputo.+ 9 Mfumuyo inauza anthu ake kuti: “Taonani! Ana a Isiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.+ 10 Tiyeni tiwachenjerere,+ kuti asapitirize kuchulukana kuopera kuti pa nthawi ya nkhondo angadzagwirizane ndi adani athu ndi kumenyana nafe n’kuchoka m’dziko lino.”

11 Choncho anawaikira akulu owayang’anira pa ntchito yawo yaukapolo, kuti aziwanyamulitsa katundu mwankhanza.+ Ndipo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramese+ kuti ikhale mosungiramo zinthu.* 12 Koma pamene anali kuwazunza kwambiri m’pamenenso anali kuwonjezeka ndi kufalikira mowirikiza, mwakuti Aiguputo anachita mantha kwambiri ndi ana a Isiraeliwo.+ 13 Chotero, Aiguputo anagwiritsa ana a Isiraeli ntchito yaukapolo mwankhanza.+ 14 Iwo anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa yaukapolo, yomwe inali yoponda matope+ ndi kuumba njerwa.* Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse m’munda,+ ndi ukapolo wa mtundu uliwonse umene anatha kuwagwiritsa ntchito mwankhanza.+

15 Kenako mfumu ya Iguputo inalamula azamba*+ achiheberi, mmodzi wotchedwa Sifira ndipo wina wotchedwa Puwa, 16 kuti: “Pamene mukuthandiza amayi achiheberi kubereka, mukaona kuti mwana akubadwayo ndi wamwamuna muzimupha, koma ngati ndi wamkazi muzimusiya wamoyo.” 17 Koma, azambawo anali oopa Mulungu+ woona, ndipo sanachite zimene mfumu ya Iguputo inawauza.+ M’malomwake, ana aamuna anali kuwasiya amoyo.+ 18 Patapita nthawi, mfumu ya Iguputo inaitana azamba aja ndi kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ana aamuna mwakhala mukuwasiya amoyo? Mwachitiranji zimenezi?”+ 19 Poyankha azambawo anauza Farao kuti: “Amayi achiheberi sali ngati amayi achiiguputo. Popeza amayi achiheberi ndi amphamvu, mzamba asanafike iwo amakhala atabereka kale.”

20 Chotero Mulungu anawadalitsa azambawo,+ ndipo ana a Isiraeli anapitiriza kuwonjezeka ndi kukhala amphamvu. 21 Choncho chifukwa chakuti azambawo anaopa Mulungu woona, m’kupita kwa nthawi iye anawadalitsa ndi mabanja awoawo.+ 22 Kenako Farao analamula anthu ake onse kuti: “Mwana aliyense wamwamuna wa Aheberi wobadwa kumene, muzim’ponya mumtsinje wa Nailo, koma mwana aliyense wamkazi muzimusiya wamoyo.”+

2 Pa nthawiyo, mwamuna wina wa fuko la Levi anakwatira mwana wa Levi.+ 2 Mkaziyo anatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, anam’bisa+ kwa miyezi itatu.+ 3 Poona kuti sakuthanso kum’bisa,+ anatenga kabokosi kagumbwa* n’kukamata phula.+ Kenako anaikamo mwanayo n’kukasiya kabokosiko pakati pa mabango+ m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo. 4 Ndiyeno mlongo wake wa mwanayo anaima chapatali ndithu kuti aone zimene zingachitikire mwanayo.+

5 Patapita kanthawi, panafika mwana wamkazi wa Farao kudzasamba mumtsinje wa Nailo. Ndipo atsikana omutumikira anali kuyenda m’mphepete mwa mtsinjewo. Kenako iye anaona kabokosi kaja kali pakati pa mabango. Nthawi yomweyo anatuma kapolo wake wamkazi kuti akakatenge.+ 6 Atabweretsa kabokosiko, anakatsegula ndipo anaona kuti muli mwana wamwamuna, ndipo anali kulira. Pamenepo anamumvera chisoni,+ ngakhale kuti anati: “Uyu ndi mmodzi wa ana a Aheberi.” 7 Zitatero, mlongo wake uja anauza mwana wa Farao kuti: “Kodi mungakonde kuti ndikakuitanireni mayi woyamwitsa wachiheberi kuti akulerereni mwanayu?” 8 Pamenepo mwana wa Faraoyo anamuyankha kuti: “Inde pita!” Nthawi yomweyo mtsikanayo anapita kukaitana mayi ake a mwanayo.+ 9 Ndiyeno mwana wa Farao anauza mayiyo kuti: “Tenga mwanayu ukandilerere ndipo ine ndizikulipira.”+ Choncho mayiyo anatenga mwanayo ndipo anamulera. 10 Mwana uja anakula. Kenako anapita naye kwa mwana wa Farao, ndipo anakhala mwana wake.+ Zitatero anam’patsa dzina lakuti Mose* n’kunena kuti: “Chifukwa chakuti ndinamuvuula m’madzi.”+

11 Tsopano m’masiku amenewo pamene Mose anali kukula ndi kukhala wamphamvu, anapita kwa abale ake kuti akaone ntchito imene anali kugwira.+ Kumeneko anaona m’bale wake wachiheberi akumenyedwa ndi Mwiguputo.+ 12 Pamenepo anayang’ana uku ndi uku ndipo anaona kuti palibe amene akumuona. Choncho anapha Mwiguputoyo ndi kum’bisa mumchenga.+

13 Koma tsiku lotsatira atapitanso, anapeza amuna awiri achiheberi akumenyana. Choncho anafunsa wolakwayo kuti: “Ukum’menyeranji mnzako?”+ 14 Poyankha iye anati: “Anakuika iwe ndani kukhala kalonga ndi woweruza wathu?+ Kodi ukufuna kundipha mmene unaphera Mwiguputo uja?”+ Pamenepo Mose anachita mantha ndipo anati mumtima mwake: “Haa! Nkhani ija yadziwika.”+

15 Patapita nthawi, Farao anaimva nkhaniyi ndipo anafuna kupha Mose.+ Koma Mose anam’thawa+ Farao ndipo anapita kukakhala kudziko la Midiyani.+ Atafika kumeneko, anakhala pachitsime. 16 Ndiyeno wansembe+ wa ku Midiyani anali ndi ana aakazi 7. Monga mwa masiku onse, iwo anafika pachitsimepo ndipo anatunga madzi ndi kuwathira m’ngalande kuti ziweto za bambo awo zimwe.+ 17 Monga mwa masiku onse, abusa anafika ndi kuwachotsapo atsikanawo. Zitatero Mose ananyamuka ndi kuthandiza atsikanawo, ndipo iye anamwetsa ziweto zawo.+ 18 Ndiyeno atsikanawo atafika kunyumba kwa bambo wawo Reueli,+ iye anadabwa ndipo anati: “Bwanji mwabwerako mwamsanga chonchi lero?” 19 Ndipo iwo anayankha kuti: “Mwiguputo+ wina watilanditsa kwa abusa, komanso watitungira madzi ndi kutimwetsera ziweto.” 20 Pamenepo iye anauza ana akewo kuti: “Nanga iyeyo ali kuti? Mwamusiyiranji? Pitani mukamuitane kuti adzadye chakudya.”+ 21 Zitatero Mose anavomereza kukhala ndi Reueli, ndipo iye anapereka Zipora+ mwana wake wamkazi kwa Mose. 22 Patapita nthawi Zipora anabereka mwana wamwamuna ndipo Mose anati: “Dzina lake akhale Gerisomu,*+ chifukwa ndine mlendo m’dziko lino.”+

23 Ndiyeno Mose atakhala kumeneko nthawi yaitali, mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma ana a Isiraeli anapitirizabe kuvutika ndi ukapolo ndi kulira modandaula.+ Iwo anapitirizabe kulirira thandizo kwa Mulungu woona chifukwa cha ukapolowo.+ 24 M’kupita kwa nthawi, Mulungu anamva+ kubuula kwawo+ ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ 25 Choncho Mulungu anayang’ana ana a Isiraeli ndipo anaona kuvutika kwawo.

3 Tsopano Mose anakhala m’busa wa ziweto za Yetero,*+ wansembe wa ku Midiyani, amene anali apongozi ake.+ Pamene anali kuweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona,+ ku Horebe.+ 2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinali kuyaka moto. Atachiyang’anitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikupsa. 3 Pamenepo Mose anati: “Ndipatuke kuti ndikaonetsetse chodabwitsa chachikulu chimenechi, kuti ndione chifukwa chake chitsamba chamingachi chikuyaka koma osapsa.”+ 4 Yehova ataona kuti Mose wapatuka kuti akaonetsetse, nthawi yomweyo Mulungu anamuitana kuchokera pakatikati pa chitsamba chamingacho, kuti: “Mose! Mose!” ndipo iye anayankha kuti: “Ndili pano.”+ 5 Ndiyeno Mulungu anati: “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, chifukwa malo waimawo ndi malo oyera.”+

6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa atate ako, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Pamenepo Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona. 7 Yehova anawonjezeranso kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo.+ 8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ 9 Taona, ndamva kulira kwa ana a Isiraeli, komanso ndaona kupondereza kumene Aiguputo akuwapondereza.+ 10 Tsopano, tamvera. Ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.”+

11 Koma Mose anayankha Mulungu woona kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?”+ 12 Pamenepo Mulungu anati: “Chifukwa ndidzakhala nawe.+ Ndipo chizindikiro chako chakuti ine ndi amene ndakutuma ndi ichi:+ Pambuyo powatulutsa anthuwo mu Iguputo, anthu inu mudzatumikira Mulungu woona paphiri lino.”+

13 Koma Mose anafunsa Mulungu woona kuti: “Nditati ndakafika kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’+ Ndikawayankhe kuti chiyani?” 14 Mulungu anamuyankha Mose kuti: “NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA.”+ Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ana a Isiraeli ukawauze kuti, ‘NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA ndiye wandituma kwa inu.’”+ 15 Kenako Mulungu anauzanso Mose kuti:

“Zimene ukauze ana a Isiraeli ndi izi, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ wandituma kwa inu.’ Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale,*+ ndipo ndicho chondikumbukirira ku mibadwomibadwo.+ 16 Pita, ukasonkhanitse akulu a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, anaonekera kwa ine+ n’kundiuza kuti: “Ndithu, ndidzakulanditsani ndi kuchitapo kanthu+ pa zonse zimene akukuchitirani mu Iguputo. 17 Ndikunenetsa kuti, ndidzakuchotsani mu nsautso+ ya Aiguputo ndi kukulowetsani m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori,+ Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.”’+

18 “Ukadzatero adzamvera mawu ako.+ Pamenepo, iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo ndi kuiuza kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tiyende ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+ 19 Koma ine ndikudziwa bwino kuti mfumu ya Iguputo sidzakulolani kupita kufikira nditaisonyeza mphamvu zanga.+ 20 Ndidzatambasula dzanja langa+ ndi kukantha Iguputo ndi ntchito zanga zonse zodabwitsa zimene ndidzazichita m’dzikolo. Pamenepo adzakulolani kuchoka.+ 21 Chotero ndidzachititsa Aiguputo kukomera mtima anthu anga, moti pochoka simudzachoka chimanjamanja.+ 22 Mkazi aliyense adzapemphe zinthu zasiliva, zagolide, ndi zovala kwa munthu wokhala naye pafupi ndi kwa mlendo wamkazi wokhala m’nyumba mwake. Zinthu zimenezi mudzaveke ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mudzatenge zinthu zambiri za Aiguputo.”+

4 Koma Mose anayankha kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira ndi kumvera mawu anga?+ Chifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekere kwa iwe.’” 2 Pamenepo Yehova anamufunsa kuti: “Chili m’dzanja lakocho n’chiyani?” ndipo Mose anayankha kuti: “Ndodo.”+ 3 Kenako iye anati: “Iponye pansi.” Anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka.+ Pamenepo Mose anayamba kuthawa. 4 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Igwire kumchira.” Choncho Mose anaigwira, ndipo inasandukanso ndodo m’dzanja lake. 5 Popitiriza Mulungu anati: “Ukachite zimenezi kuti akakhulupirire kuti Yehova Mulungu wa makolo awo,+ Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ anaonekera kwa iwe.”+

6 Kenako Yehova anamuuzanso kuti: “Lowetsa dzanja lako m’malaya pachifuwa.” Choncho Mose analowetsa dzanja lake m’malaya. Koma politulutsa, dzanja lakelo linali litachita khate, ndipo linaoneka loyera kwambiri ngati chipale chofewa.+ 7 Ndiyeno Mulungu anati: “Lowetsanso dzanja lako m’malayamo.” Choncho analowetsanso dzanja lake m’malaya. Atalitulutsa anaona kuti lakhalanso bwino ngati poyamba.+ 8 Mulungu anapitiriza kuti: “Ngati sakakukhulupirira ndi kulabadira chizindikiro choyamba, akakhulupirira chizindikiro chachiwirichi.+ 9 Komabe ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwirizi ndi kumvera mawu ako,+ ukatenge madzi a mumtsinje wa Nailo n’kuwathira panthaka youma. Ndipo madziwo, amene ukatenge mumtsinje wa Nailo, adzasanduka magazi panthakapo. Ndithu adzasanduka magazi.”+

10 Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Pepani Yehova, ine sinditha kulankhula, kuyambira kalekale, kapena pamene mwalankhula ndi ine mtumiki wanu. Pakuti ndimalankhula movutikira ndipo ndine wa lilime lolemera.”+ 11 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?+ 12 Choncho pita. Ine ndidzakhala nawe polankhula ndipo ndidzakuuza zonena.”+ 13 Koma Mose anati: “Pepani Yehova. Chonde, tumizani wina aliyense amene mungam’tumize.” 14 Zitatero, Yehova anamukwiyira kwambiri Mose ndipo anati: “Kodi Aroni Mlevi si m’bale wako?+ Ndikudziwa kuti amatha kulankhula. Ndiponso, iye ali m’njira kudzakuchingamira. Akakuona, adzakondwera kwambiri mumtima mwake.+ 15 Ukalankhule naye ndi kumuuza zokanena.+ Ineyo ndidzakhala ndi iwe pamodzi ndi iye pamene mukulankhula,*+ ndipo ndidzakuuzani zochita.+ 16 Iyeyo ndiye azikalankhula kwa anthu m’malo mwa iwe.+ Choncho adzakhala ngati kamwa lako, ndipo iwe udzakhala ngati Mulungu kwa iye.+ 17 Ndipo ndodo iyi izikakhala m’dzanja lako kuti ukaigwiritse ntchito pochita zizindikiro.”+

18 Chotero Mose anapita kwa Yetero apongozi ake ndi kuwauza kuti:+ “Ndikufuna kupita kwa abale anga ku Iguputo kuti ndikaone ngati akali moyo.”+ Choncho, Yetero anayankha Mose kuti: “Pita mu mtendere.”+ 19 Ndiyeno Yehova anamuuza Mose ali ku Midiyani kuti: “Nyamuka, bwerera ku Iguputo, chifukwa onse amene anali kufuna moyo wako anafa.”+

20 Kenako Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake ndi kuwakweza pabulu, ndi kuyamba ulendo wobwerera ku Iguputo. Komanso, Mose anatenga ndodo ya Mulungu woona m’dzanja lake.+ 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ 22 Choncho ukamuuze Farao kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Isiraeli ndi mwana wanga wamwamuna, mwana wanga woyamba kubadwa.+ 23 Ndipo ndikukuuza kuti: Lola mwana wanga apite kuti akanditumikire. Koma ngati ukukana kumulola kuti apite, taona ndidzapha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba kubadwa.”’”+

24 Ndiyeno ali pa ulendowo, atafika pamalo ogona,+ Yehova anakumana naye,+ ndipo anali kufunafuna njira yoti amuphere.+ 25 Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa n’kudula khungu+ la mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pamapazi ake n’kunena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.” 26 Atatero, Mulungu anam’siya mwanayo. Pamenepo Zipora anati: “Mkwati wa magazi,” chifukwa cha mdulidwewo.

27 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Pita kuchipululu+ kukachingamira Mose.” Chotero Aroni ananyamuka ndipo anakumana ndi Mose paphiri la Mulungu woona,+ nam’psompsona. 28 Atakumana, Mose anauza Aroni mawu onse a Yehova, yemwe anam’tuma.+ Anamuuzanso zizindikiro zonse zimene anam’lamula kuchita.+ 29 Kenako Mose ndi Aroni anapita kukasonkhanitsa akulu onse a ana a Isiraeli.+ 30 Pamenepo Aroni anawauza mawu onse amene Yehova anauza Mose,+ ndipo iye anachita zizindikiro+ pamaso pa anthuwo. 31 Zitatero anthuwo anakhulupirira+ Mose. Atamva kuti Yehova wacheukira+ ana a Isiraeli, ndi kutinso waona nsautso yawo,+ anagwada ndi kuweramira pansi.+

5 Kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kumuuza kuti:+ “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lolani anthu anga apite m’chipululu kuti akachite chikondwerero.’”+ 2 Koma Farao anati: “Yehova ndani+ kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono,+ komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.”+ 3 Koma iwo anati: “Mulungu wa Aheberi walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tipite ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.+ Ngati sititero, adzatipha ndi mliri kapena lupanga.”+ 4 Pamenepo mfumu ya Iguputo inawauza kuti: “N’chifukwa chiyani iwe Mose ndi Aroni mukufuna kuti anthu asiye ntchito zawo?+ Bwererani ku ukapolo wanu!”+ 5 Farao anapitiriza kuti: “Anthu amenewa ndi ambiri m’dziko lino,+ ndipo inu mukufuna kuwasiyitsa ntchito yawo ya ukapolo.”+

6 Tsiku lomwelo Farao analamula amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo mwankhanza, ndi akapitawo a anthuwo+ kuti: 7 “Anthu amenewa musawapezerenso udzu woumbira njerwa+ ngati kale. Muwasiye azikafuna okha udzu umenewo. 8 Komanso, muwauze kuti chiwerengero cha njerwa zofunika chikhale chakale chomwe chija. Musawachepetsere chiwerengerocho, chifukwa ayamba ulesi.+ N’chifukwa chake akulira kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu!’+ 9 Agwiritseni ntchito yakalavulagaga anthu amenewa ndipo muonetsetse kuti sakuchita ulesi ndi kumvera zabodza.”+

10 Choncho amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo,+ pamodzi ndi akapitawo anapita kwa Aisiraeli n’kukawauza kuti: “Mverani zimene Farao wanena, ‘Sindikupatsaninso udzu woumbira njerwa. 11 Inuyo muzikafuna nokha udzu kulikonse kumene mungaupeze, koma ntchito yanu sichepetsedwa ngakhale pang’ono.’”+ 12 Chotero, anthu anali balalabalala m’dziko lonse la Iguputo kukafuna mapesi m’malo mwa udzu. 13 Motero amene anali kuwagwiritsa ntchito aja anali kuwakakamiza+ kugwira ntchito ponena kuti: “Muzimaliza ntchito yanu. Aliyense azimaliza ntchito yake tsiku lililonse, ngati mmene munali kuchitira pamene udzu unali kupezeka.”+ 14 Kenako oyang’anira ntchito+ a Farao anamenya+ akapitawo a ana a Isiraeli amene iwo anawaika, n’kumati: “N’chifukwa chiyani dzulo ndi lero simunamalize kuumba njerwa+ zimene munauzidwa ngati mmene munali kuchitira kale?”+

15 Zitatero akapitawo+ a ana a Isiraeli anapita kwa Farao ndi kumudandaulira kuti: “N’chifukwa chiyani atumiki anu mukuwachitira zimenezi? 16 Ife atumiki anu sitikupatsidwa udzu, koma akutiuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ ndipo tikumenyedwa ngakhale kuti olakwa ndi anthu anu.”+ 17 Koma iye anati: “Mukuchita ulesi, mukuchita ulesi!+ N’chifukwa chake mukunena kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’+ 18 Choncho pitani, katumikireni! Ngakhale kuti sakupatsani udzu, komabe chiwerengero cha njerwa zimene muziumba sichisintha.”+

19 Pamenepo akapitawo a ana a Isiraeli anaona kuti zinthu zawaipira atamva mawu akuti:+ “Musachepetse ngakhale pang’ono chiwerengero cha njerwa zimene aliyense amaumba tsiku ndi tsiku.”+ 20 Zitatero anakumana ndi Mose ndi Aroni,+ amene anali kudikira akapitawowa kuti aonane nawo pamene amachokera kwa Farao. 21 Nthawi yomweyo iwo anati: “Yehova aone zimene mwachitazi ndipo akuweruzeni,+ chifukwa mwatinunkhitsa+ pamaso pa Farao ndi atumiki ake, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.”+ 22 Pamenepo Mose anatembenukira kwa Yehova+ n’kunena kuti: “Yehova, n’chifukwa chiyani mwadzetsa zoipa pa anthu awa?+ Mwanditumiranji ine?+ 23 Kuchokera pamene ndinapita kukalankhula ndi Farao m’dzina lanu,+ iye wachitira anthu awa zinthu zoipa,+ ndipo inu simunalanditse anthu anu.”+

6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+

2 Mulungu ananenanso kwa Mose kuti: “Ine ndine Yehova.+ 3 Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo. 4 Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene anali kukhalamo monga alendo.+ 5 Motero ineyo ndamva kubuula kwa ana a Isiraeli,+ amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+

6 “Choncho uwauze ana a Isiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndithu, ndidzakutulutsani mu Iguputo ndi kukuchotserani goli lawo, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wawo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+ 7 Chotero ndidzakutengani kukhala anthu anga,+ ndi kukusonyezani kuti ndine Mulungu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndidzakutulutsani mu Iguputo, ndi kukuchotserani goli lawo.+ 8 Ine ndidzakulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira+ Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, nditakweza dzanja langa. Ndidzakupatsani dzikolo kukhala lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+

9 Kenako Mose analankhula mawu amenewa kwa ana a Isiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+

10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11 “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo,+ ukamuuze kuti alole ana a Isiraeli kutuluka m’dziko lake.”+ 12 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu ana a Isiraeli sanandimvere,+ nanga Farao akandimvera bwanji?+ Pakuti ndimalankhula movutikira.”*+ 13 Koma Yehova anapitirizabe kuuza Mose ndi Aroni, kuti apereke lamulo kwa ana a Isiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.+

14 Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo a Aisiraeli. Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Rubeni.+

15 Ndipo ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wachikanani.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Simiyoni.+

16 Awa ndi mayina a ana aamuna a Levi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo:+ Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137.

17 Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+

18 Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.

19 Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi.+

Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+

20 Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mlongo wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anam’berekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137.

21 Ndipo ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri.

22 Ndipo ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana ndi Sitiri.+

23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anam’berekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+

24 Ndipo ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa ndiwo anali mabanja a Kora.+

25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni,+ anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anam’berekera Pinihasi.+

Amenewa ndiwo atsogoleri a mabanja a m’fuko la Levi, malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+

26 Umenewu ndiwo mzere wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti:+ “Tulutsani ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo malinga ndi makamu awo.”+ 27 Mose ndi Aroni amenewa ndi amene analankhula kwa Farao mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli mu Iguputo.+

28 Choncho pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose m’dziko la Iguputo,+ 29 Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova.+ Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.” 30 Pamenepo Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira, ndiye Farao akandimvera bwanji?”+

7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Taona, ndakuika kuti ukhale Mulungu kwa Farao,+ ndipo Aroni m’bale wako akhala mneneri wako.+ 2 Iwe uzimuuza zonse zimene ndizikulamula,+ koma Aroni m’bale wako azikulankhulira kwa Farao,+ ndipo adzaloladi ana a Isiraeli kuchoka m’dziko lake.+ 3 Koma ine ndidzamusiya Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.+ 4 Komabe Farao sadzakumverani,+ motero ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa makamu anga,+ anthu anga,+ ana a Isiraeli,+ m’dziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+ 5 Pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzatambasula dzanja langa ndi kukantha Iguputo.+ Motero ndidzatulutsa ana a Isiraeli m’dzikolo.”+ 6 Choncho Mose ndi Aroni anachitadi monga momwe Yehova anawalamulira.+ Anachitadi momwemo.+ 7 Pa nthawi imene analankhula ndi Farao, Mose anali ndi zaka 80 ndipo Aroni anali ndi zaka 83.+

8 Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 9 “Farao akakanena kuti, ‘Ndisonyezeni chozizwitsa,’+ iweyo ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako+ ndi kuiponya patsogolo pa Farao.’ Akakatero, idzasanduka njoka yaikulu.”+ 10 Chotero Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kuchita ndendende mmene Yehova anawalamulira. Pamenepo Aroni anaponya ndodo yake patsogolo pa Farao ndi atumiki ake, ndipo ndodoyo inasanduka njoka yaikulu. 11 Komabe, Farao nayenso anaitana amuna ake anzeru ndi amatsenga.+ Choncho ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo.+ 12 Aliyense wa iwo anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka njoka zazikulu. Koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo. 13 Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake,+ ndipo sanawamvere, monga momwe Yehova ananenera.

14 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Farao waumitsa mtima wake.+ Iye wakana kuti ana a Isiraeli achoke.+ 15 M’mawa upite kwa Farao. Iyetu adzakhala akupita kumtsinje.+ Choncho iweyo ukaime poti ukathe kukumana naye m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo,+ ndipo udzatenge ndodo imene inasanduka njoka ija.+ 16 Kumeneko ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wandituma kwa iwe+ ndi uthenga wonena kuti: “Lola anthu anga kuchoka kuti akanditumikire m’chipululu,”+ koma kufikira tsopano sukundimvera. 17 Yehova wanena kuti:+ “Ndimenya madzi a mumtsinje wa Nailo+ ndi ndodo imene ili m’dzanja langa, ndipo madzi asanduka magazi.+ Zikatero udziwa kuti ine ndine Yehova.+ 18 Nsomba zimene zili mumtsinje wa Nailo zifa,+ ndipo mtsinje wa Nailo ununkha,+ moti Aiguputo safunanso kumwa madzi ake.”’”+

19 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako+ ndi kuloza madzi a mu Iguputo. Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo zochokera kumtsinje wa Nailo, zithaphwi zawo,+ ndi maiwe awo onse kuti asanduke magazi.’ Pamenepo madzi a m’dziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi a m’mitsuko yawo ya mtengo ndi ya mwala adzakhala magazi.” 20 Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita zomwezo,+ monga momwe Yehova anawalamulira.+ Ndipo Aroni anatenga ndodo yake ndi kumenya madzi a mumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona.+ Pamenepo madzi onse a mumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+ 21 Zitatero nsomba za mumtsinje wa Nailo zinafa,+ ndipo mtsinje wa Nailo unayamba kununkha. Aiguputo sanathenso kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo.+ M’dziko lonse la Iguputo munali magazi okhaokha.

22 Komano, ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo,+ moti Farao anaumitsabe mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga Yehova ananenera.+ 23 Pamenepo Farao anabwerera kunyumba kwake, ndipo sanafune m’pang’ono pomwe kumvanso za nkhani imeneyi.+ 24 Kenako Aiguputo onse anayamba kukumba zitsime m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sakanatha kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo.+ 25 Kuchokera pamene Yehova anasandutsa madzi a mumtsinje wa Nailo kukhala magazi, panadutsa masiku 7.

8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 2 Ngati upitiriza kukana kuti apite, ndigwetsera dziko lako lonse mliri wa achule.+ 3 Achulewo adzachuluka kwambiri mumtsinje wa Nailo, ndipo adzatuluka mumtsinjemo ndi kulowa m’nyumba yako, m’chipinda chako chogona, pabedi pako, ndiponso m’nyumba za atumiki ako, za anthu ako, m’mauvuni ako, ndi m’ziwiya zako zokandiramo ufa.+ 4 Ndipo achulewo adzabwera kwa iwe, anthu ako ndi atumiki ako onse.”’”+

5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tambasula dzanja lako ndi kulozetsa ndodo+ yako kumitsinje, kungalande zochokera kumtsinje wa Nailo ndi kuzithaphwi, kuti achule atuluke mmenemo ndi kubwera pamtunda m’dziko lonse la Iguputo.’” 6 Pamenepo Aroni anatambasula dzanja lake ndi kuloza madzi onse a mu Iguputo, ndipo achule anayamba kutuluka ndi kudzaza dziko lonse la Iguputo. 7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda m’dziko la Iguputo.+ 8 Patapita nthawi, Farao anaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Chondererani Yehova+ kuti achotse achule pa ine ndi anthu anga, pakuti ndikufuna kulola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”+ 9 Ndiyeno Mose anauza Farao kuti: “Munene ndinu kuti ndikachonderere liti kwa Mulungu m’malo mwa inu, m’malo mwa atumiki anu, ndi anthu anu, kuti iye achotse achule pa inu ndi m’nyumba zanu. Koma achulewo adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.” 10 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Mawa.” Ndiyeno Mose anati: “Zidzachitika monga mwa mawu anu, kuti mudziwe kuti palibenso wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,+ 11 popeza achule adzachoka pa inu, panyumba zanu, pa atumiki anu ndi pa anthu anu. Adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”+

12 Chotero Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa Farao, ndipo Mose anafuulira Yehova+ kuti achotse achule amene Iye anagwetsera Farao. 13 Pamenepo Yehova anachita monga mmene Mose anapemphera,+ ndipo achule amene anali m’nyumba, m’mabwalo ndi m’minda anayamba kufa. 14 Aiguputo anayamba kuunjika achulewo milumilu, ndipo dziko lonselo linayamba kununkha.+ 15 Farao ataona kuti mliri wa achulewo watha, anaumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga momwe Yehova ananenera.+

16 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo+ yako ndi kumenya fumbi lapansi, kuti likhale ntchentche zoluma m’dziko lonse la Iguputo.’” 17 Iwo anachitadi zomwezo. Choncho Aroni anatambasula dzanja lake ndi kumenya fumbi lapansi ndi ndodo yake, ndipo ntchentchezo zinayamba kuluma anthu ndi nyama zomwe. Fumbi lonse la m’dziko la Iguputo linasanduka ntchentche zoluma.+ 18 Ndipo ansembe ochita zamatsenga, anafunanso kuti apange ntchentche zoluma mwa matsenga awo,+ koma analephera.+ Ndipo ntchentchezo zinali kuluma anthu ndi nyama zomwe. 19 Ataona zimenezi ansembe ochita zamatsenga anauza Farao kuti: “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!”+ Koma Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere, monga momwe Yehova ananenera.

20 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire m’mawa kwambiri kukakumana ndi Farao.+ Iyetu adzapita kumtsinje, ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 21 Koma ngati sulola anthu anga kupita, taona nditumiza tizilombo touluka toyamwa magazi+ kwa iweyo, atumiki ako, anthu ako ndi m’nyumba zanu. Ndipo nyumba za mu Iguputo zidzangodzaziratu ndi tizilombo timeneti, komanso pena paliponse pamene pali anthu. 22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga, kuti kusakhale tizilombo toyamwa magazi.+ Ndidzatero kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, ndipo ndili ndi mphamvu padziko lonse lapansi.+ 23 Ndipo ndidzaika malire pakati pa anthu anga ndi anthu ako.+ Mawa chizindikiro chimenechi chidzachitika.”’”

24 Yehova anachitadi zimenezo, moti tizilombo touluka toyamwa magazi tinali ponseponse m’nyumba ya Farao, m’nyumba za atumiki ake ndi m’dziko lonse la Iguputo.+ Dziko linaipa chifukwa cha tizilombo timeneto.+ 25 Zitatero, Farao anaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Pitani, kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu m’dziko lomwe lino.”+ 26 Koma Mose anati: “Sikoyenera kuchita zimenezo, chifukwa mwina chinthu chomwe tingapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu chingakhale chonyansa kwa Aiguputo.+ Kodi Aiguputo sadzatiponya miyala ngati tingapereke nsembe chinthu chonyansa pamaso pawo? 27 Ife tidzapita ulendo wamasiku atatu m’chipululu, ndipo kumeneko tikapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, monga momwe watiuzira.”+

28 Ndiyeno Farao anati: “Ineyo ndikulolani kupita,+ ndipo mukaperekadi nsembe kwa Yehova Mulungu wanu m’chipululu,+ koma musapite kutali kwambiri. Ndichonderereni kwa Mulungu wanu.”+ 29 Pamenepo Mose anati: “Mmene ndikuchoka pano, ndikukachonderera Yehova ndipo mawa tizilomboti tichoka pa Farao, atumiki ake ndi anthu ake. Koma Farao asatipusitsenso mwa kusalola anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Yehova.”+ 30 Zitatero Mose anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+ 31 Choncho Yehova anachita monga momwe Mose anapemphera,+ ndipo tizilomboto tinachoka pa Farao, atumiki ake ndi anthu ake.+ Sipanatsale kachilombo ngakhale n’kamodzi komwe. 32 Koma pamenepanso, Farao anaumitsa mtima wake, ndipo sanalole anthuwo kuchoka.+

9 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti,+ ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire. 2 Koma ukapitiriza kukana kuti asapite, n’kuwaumirirabe,+ 3 dziwa kuti, dzanja la Yehova+ lipha ziweto zanu zonse.+ Mliri waukulu kwambiri ugwera mahatchi,* abulu, ngamila, ng’ombe ndi nkhosa.+ 4 Ndipo Yehova adzaika malire pakati pa ziweto za Isiraeli ndi ziweto za Iguputo, moti palibe chiweto cha ana a Isiraeli chimene chidzafa.”’”+ 5 Komanso, Yehova anatchuliratu nthawi, kuti: “Mawa, Yehova adzachita zimenezi m’dzikoli.”+

6 Mogwirizana ndi mawu ake, Yehova anachitadi zimenezi tsiku lotsatira, ndipo ziweto zamitundu yonse za Aiguputo zinayamba kufa,+ koma palibe chiweto ngakhale chimodzi cha ana a Isiraeli chimene chinafa. 7 Pamenepo Farao anatumiza atumiki ake kukaona, ndipo anapezadi kuti palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake,+ osalola ana a Isiraeli kupita.

8 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Tengani mwaye wa mu uvuni wodzaza manja anu awiri,+ ndipo Mose auponye m’mwamba, Farao akuona. 9 Pamenepo udzachuluka ndi kugwa ngati fumbi padziko lonse la Iguputo. Ukatero udzayambitsa zithupsa zimene zizidzaphulika+ pa anthu ndi nyama zomwe, m’dziko lonse la Iguputo.”

10 Choncho iwo anatenga mwaye wa mu uvuni ndi kuima pamaso pa Farao. Pamenepo Mose anauponya m’mwamba, ndipo unayambitsa zithupsa zomaphulika,+ pa anthu ndi nyama. 11 Ndipo ansembe ochita zamatsenga sanathe kuonekera pamaso pa Mose chifukwa cha zithupsazo, popeza zinatuluka pa ansembewo ndi pa Aiguputo onse.+ 12 Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga momwe Yehova anauzira Mose.+

13 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ukalawirire m’mawa kwambiri kukaonana ndi Farao,+ ndipo ukamuuze kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 14 Ukakana, nditumiza miliri yanga yonse pa iwe, pa atumiki ako ndi anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wofanana ndi ine padziko lonse lapansi.+ 15 Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mliri, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi.+ 16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+ 17 Kodi ukudzikwezabe pa anthu anga, pokana kuwalola kuti achoke?+ 18 Taona, mawa pa nthawi ngati ino ndigwetsa mvula yamphamvu kwambiri ya matalala, matalala amene sanayambe agwapo mu Iguputo m’mbiri yake yonse mpaka lero.+ 19 Tsopano tumiza atumiki ako kuti asonkhanitse ziweto zako zonse ndi zinthu zako zonse zimene zili kunja ndi kuzilowetsa m’malo otetezeka. Koma munthu aliyense amene adzapezeke kunja osati m’nyumba, ndi nyama iliyonse imene idzapezeke kunja, matalala+ adzawagwera ndipo adzafa.”’”

20 Aliyense amene anaopa mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao anaonetsetsa kuti ziweto zake ndi antchito ake athawira m’nyumba.+ 21 Koma aliyense amene sanalabadire mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.+

22 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako+ ndi kuloza kumwamba, kuti matalala+ agwe m’dziko lonse la Iguputo, kuti agwere anthu, nyama ndi zomera zonse m’dziko la Iguputo.” 23 Ndipo Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala+ ndi moto padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala padziko la Iguputo. 24 Motero panagwa matalala, ndipo panali kuwalima moto. Panagwa matalala amphamvu kwambiri amene sanaonekepo n’kale lonse m’dziko lonse la Iguputo.+ 25 Matalalawo anawononga dziko lonse la Iguputo. Anawononga china chilichonse, munthu kapena nyama, ndi mitundu yonse ya zomera zam’munda. Anagwetsanso mitundu yonse ya mitengo.+ 26 Koma kudera la Goseni kokha, kumene kunali ana a Isiraeli, sikunagwe matalala.+

27 Kenako Farao anatumiza atumiki ake kukaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Tsopano ndachimwa.+ Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 M’chonderereni Yehova kuti aletse mabingu ndi matalala ake.+ Pamenepo ndikulolani kupita, ndipo simukhalanso kuno.” 29 Choncho Mose anamuyankha kuti: “Ndikangotuluka mumzinda uno, ndikweza manja anga kwa Yehova.+ Mabingu ndi matalala asiya, kuti mudziwe kuti dziko lapansi ndi la Yehova.+ 30 Koma ndikudziwa kuti ngakhale pamenepo inuyo ndi atumiki anu simudzasonyeza kuopa Yehova Mulungu.”+

31 Pa nthawi imeneyo mbewu za fulakesi* ndi balere zinawonongeka, chifukwa balere anali atacha ndipo fulakesi anali atachita maluwa.+ 32 Koma tirigu*+ sanawonongeke, chifukwa amacha mochedwa. 33 Ndiyeno Mose anachoka pamaso pa Farao, n’kutuluka mumzindawo. Kenako anakweza manja ake kwa Yehova, ndipo mabingu ndi matalala zinasiya, mvulanso inasiya kugwa padziko lapansi.+ 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zasiya, anachimwanso ndipo anaumitsa mtima wake,+ iyeyo ndi atumiki ake. 35 Chotero Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti ana a Isiraeli apite, monga momwedi Yehova ananenera kudzera mwa Mose.+

10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao pakuti ndalola iye pamodzi ndi atumiki ake kuumitsa mitima yawo,+ kuti ndichite zizindikiro zanga pamaso pake.+ 2 Ndachita zimenezi kuti mufotokozere ana anu, ndi ana a ana anu, mmene ndakhaulitsira Iguputo ndi zizindikiro zimene ndachitira Aiguputo.+ Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+

3 Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kumuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti, ‘Udzakana kundigonjera kufikira liti?+ Lola anthu anga apite kuti akanditumikire. 4 Ukapitiriza kukaniza anthu anga kupita, mawa ndikutumizira dzombe m’dziko lako.+ 5 Dzombelo lidzakuta nthaka yonse ndipo simudzatha kuona dothi. Lidzadya chilichonse chotsalira. Ndithu, lidzadya chilichonse chimene matalala anakusiyirani. Ndipo lidzadya mitengo yanu yonse imene yaphuka.+ 6 Ndipo dzombelo lidzadzaza m’nyumba zanu, m’nyumba zonse za atumiki anu ndi m’nyumba za mu Iguputo monse. Lidzadzaza m’nyumbazi mpaka kufika poti makolo anu ndi makolo a makolo anu sanaonepo chibadwire chawo.’”+ Atatero, Mose anachoka pamaso pa Farao.+

7 Pamenepo atumiki a Farao anamuuza kuti: “Kodi munthu uyu akhala ngati msampha kwa ife kufikira liti?+ Lolani anthuwa apite kuti akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simukudziwabe kuti Iguputo wawonongeka?”+ 8 Zitatero anabweretsanso Mose ndi Aroni kwa Farao ndipo iye anati: “Pitani, katumikireni Yehova Mulungu wanu.+ Ndani kwenikweni amene akupita?” 9 Pamenepo Mose anati: “Tipita ndi achinyamata athu ndi achikulire omwe. Tipita ndi ana athu aamuna ndi ana athu aakazi+ pamodzi ndi nkhosa ndi ng’ombe zathu,+ chifukwa tikukachitira Yehova chikondwerero.”+ 10 Farao anawayankha kuti: “Ngati ndingalole n’komwe kuti inu pamodzi ndi ana anu mupite,+ ndiye kuti Yehova alidi ndi inu. Ndikudziwatu kuti zolinga zanu ndi zoipa.+ 11 Sizitheka! Pitani amuna amphamvu nokhanokha, mukatumikire Yehova chifukwa ndi zimene mukufuna.” Atanena mawu amenewa, anawachotsa pamaso pa Farao.+

12 Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula+ dzanja lako ndi kuloza dziko la Iguputo, kuti dzombe ligwe m’dziko lonselo ndi kudya zomera zonse za m’dzikomo, chilichonse chimene matalala anasiya.”+ 13 Pomwepo Mose analoza dziko lonse la Iguputo ndi ndodo yake, ndipo Yehova anachititsa mphepo yochokera kum’mawa+ kuwomba padziko lonselo, usana wonse ndi usiku wonse. M’mawa kutacha mphepoyo inabweretsa dzombe. 14 Ndipo dzombelo linayamba kufika m’dziko lonse la Iguputo ndi kutera m’madera onse a dzikolo.+ Linawasautsa kwambiri.+ Dzombe ngati limeneli linali lisanagwepo n’kale lonse ndipo sipadzagwanso lina ngati limeneli. 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+

16 Mwamsanga Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni n’kuwauza kuti: “Ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso ndachimwira inu.+ 17 Chotero ndikhululukireni+ tchimo langa kamodzi kokha kano, ndipo chondererani+ Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.” 18 Pamenepo anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+ 19 Atatero Yehova anasintha mphepo yamphamvuyo kuti iziwomba kuchokera kumadzulo ndipo inatenga dzombelo ndi kulithira m’Nyanja Yofiira. Motero m’dera lonse la Iguputo simunatsale dzombe ngakhale limodzi. 20 Koma Yehova analola Farao kuumitsabe mtima wake,+ ndipo sanalole ana a Isiraeli kuchoka.

21 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba+ kuti m’dziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.” 22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba, ndipo m’dziko lonse la Iguputo munachita mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+ 23 Anthu sanathe kuonana ndipo palibe anachoka pakhomo pake kwa masiku atatu. Koma kumene ana onse a Isiraeli anali kukhala kunali kuwala.+ 24 Zitatero Farao anaitana Mose ndi kumuuza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova.+ Koma nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu simupita nazo. Ana anu pitani nawo.”+ 25 Koma Mose anati: “Inuyo mutipatse nyama zokapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kuti tikazipereke kwa Yehova Mulungu wathu.+ 26 Komanso ziweto zathu tipita nazo.+ Sitidzasiya chiweto ngakhale chimodzi, chifukwa tiyenera kukatengapo zina ndi kukazigwiritsa ntchito polambira Yehova Mulungu wathu.+ Pakali pano sitikudziwa kuti tikapereka chiyani polambira Yehova mpaka titakafika kumeneko.”+ 27 Pamenepo Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli achoke.+ 28 Choncho Farao anauza Mose kuti: “Choka!+ Samala! Ndisadzakuonenso, chifukwa ndikadzangokuonanso udzafa.”+ 29 Ndipo Mose anayankha kuti: “Chabwino. Sindidzayesanso kuonana nanu.”+

11 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndikanthe nawo Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka m’dziko lino.+ Pokulolani kuchoka ndi zonse zimene muli nazo, adzachita kukupitikitsani.+ 2 Tsopano uza anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnzake zinthu zasiliva ndi zagolide.”+ 3 Pamenepo Yehova anachititsa Aiguputo kukomera mtima Aisiraeli.+ Nayenso Mose analemekezeka kwambiri m’dziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.+

4 Choncho Mose anati: “Yehova wanena kuti, ‘Pakati pa usiku ndidzalowa mu Iguputo,+ 5 ndipo mwana aliyense woyamba kubadwa+ m’dziko la Iguputo adzafa. Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa kapolo wamkazi wokhala pamphero ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+ 6 Mudzakhala kulira kwakukulu m’dziko lonse la Iguputo, kulira kumene sikunachitikepo, ndiponso kumene sikudzachitikanso.+ 7 Koma galu sadzauwa aliyense wa ana a Isiraeli, sadzauwa munthu kapena chiweto,+ kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira ana a Isiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+ 8 Ndipo atumiki anu onsewa adzatsika ndi kubwera kwa ine, n’kundigwadira ndi kundiweramira.+ Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’ Zitatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.

9 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Farao sadzakumverani inu.+ Izi zili choncho kuti ndichite zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.”+ 10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao.+ Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, moti sanalole ana a Isiraeli kuchoka m’dziko lake.+

12 Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni m’dziko la Iguputo kuti: 2 “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba* wa miyezi ya pa chaka. Chaka chanu chiziyamba ndi mwezi uno.+ 3 Uzani khamu lonse la Isiraeli kuti, ‘Pa tsiku la 10 la mwezi uno mabanja onse ochokera mwa kholo limodzi atenge nkhosa imodziimodzi,+ banja lililonse litenge nkhosa imodzi. 4 Koma ngati banja lili laling’ono moti silingamalize kudya nkhosa yonseyo, mutu wa banja limenelo agawane ndi munthu wokhala naye pafupi m’nyumba mwake, mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu. Aliyense mum’gawire nkhosayo malinga ndi mmene amadyera. 5 Nkhosa yanuyo ikhale yopanda chilema,+ yamphongo, yachaka chimodzi.+ Mungatenge mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi. 6 Nkhosayo muisunge kufikira tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Isiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+ 7 Atatero adzatenge magazi ndi kuwaza pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo ndi pafelemu la pamwamba pa chitseko. Adzachite zimenezi panyumba zimene mudzadyeremo nkhosayo.+

8 “‘Adzadye nyamayo usiku umenewu.+ Idzakhale yowotcha ndipo adzaidye pamodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa+ ndi masamba owawa.+ 9 Musadzaidye yaiwisi kapena yowiritsa, yophika ndi madzi, koma mudzadye yowotcha pamoto. Mudzawotche mutu wake pamodzi ndi ziboda ndiponso zam’mimba. 10 Koma musadzasiye nyama iliyonse kuti ifike m’mawa. Iliyonse yotsala kufika m’mawa mudzaipsereze pamoto.+ 11 Kudya kwake mudzadye motere, mudzakhale mutamangirira m’chiuno mwanu,+ mutavala nsapato+ ndiponso mutatenga ndodo m’dzanja lanu. Muzidzadya mofulumira. Ameneyu ndi pasika* wa Yehova.+ 12 Ine ndidzadutsa m’dziko la Iguputo usiku umenewo+ ndi kupha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka ziweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova.+ 13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo.

14 “‘Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi. 15 Muzidya mkate wopanda chofufumitsa masiku 7. Tsiku loyamba muzichotsa m’nyumba zanu mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa chifukwa aliyense wakudya mkate wokhala ndi chofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7,+ munthu wotero adzaphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli.+ 16 Pa tsiku loyamba muzidzachita msonkhano wopatulika, ndipo pa tsiku la 7 muzidzachitanso msonkhano wopatulika.+ Masiku amenewa musamadzagwire ntchito.+ Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.+

17 “‘Muzidzasunga chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ chifukwa pa tsiku limeneli ndidzatulutsa makamu anu m’dziko la Iguputo. Muzidzasunga tsiku limeneli m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 18 M’mwezi woyamba, tsiku la 14 la mwezi umenewo, madzulo muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa, mpaka kukafika madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.+ 19 Musamadzapezeke mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa m’nyumba zanu kwa masiku 7, chifukwa aliyense wakudya mtanda wokhala ndi chofufumitsa, kaya ndi mlendo kapena mbadwa ya Isiraeli,+ munthu ameneyo adzaphedwa kuti asakhalenso mu khamu la Isiraeli.+ 20 Musamadzadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. M’nyumba zanu zonse muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa.’”

21 Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli+ ndi kuwauza kuti: “Sankhani nkhosa ndi mbuzi* malinga ndi mabanja anu, muiphere nsembe ya pasika.+ 22 Mukatero mutenge kamtengo ka hisope+ n’kukaviika m’beseni la magazi ndi kuwaza pafelemu la pamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwaze pamafelemu awiri a m’mbali mwa khomo. Aliyense asatuluke m’nyumba yake mpaka m’mawa. 23 Pamenepo Yehova akamapita kukapha Aiguputo ndi mliri, akaona magazi pamafelemu a pamwamba pa zitseko zanu ndi mafelemu awiri a m’mbali mwa khomo, Yehova adzapitirira khomo limenelo ndipo sadzalola chiwonongeko kulowa m’nyumba zanu ndi kukuphani.+

24 “Choncho muzisunga zimenezi, limeneli ndi langizo+ kwa inu ndi kwa ana anu mpaka kalekale.+ 25 Ndipo mukadzalowa m’dziko limene Yehova adzakupatsani, monga mmene ananenera, pamenepo muzidzachita mwambo umenewu.+ 26 Ndiyeno ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’+ 27 pamenepo mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya pasika kwa Yehova,+ amene anapitirira nyumba za ana a Isiraeli mu Iguputo pamene anali kupha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’”

Atatero, anthu anagwada ndi kuweramira pansi.+ 28 Pamenepo ana a Isiraeli anachoka ndi kukachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aroni.+ Anachitadi momwemo.

29 Chotero pakati pa usiku, Yehova anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa mkaidi amene ali m’ndende yapansi, ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+ 30 Zitatero Farao, atumiki ake onse ndi Aiguputo onse anadzuka pakati pa usiku. Ndipo anthu anayamba kulira kwambiri m’dziko lonse la Iguputo,+ chifukwa panalibe banja ngakhale limodzi limene linalibe maliro. 31 Nthawi yomweyo Farao anaitanitsa+ Mose ndi Aroni usiku, ndipo anati: “Nyamukani, chokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi ana onse a Isiraeli. Pitani, katumikireni Yehova, monga momwe mwanenera.+ 32 Tengani nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu monga mwanenera,+ ndipo pitani. Komanso mukandipemphere madalitso.”

33 Choncho Aiguputo anaumiriza anthuwo kuti achoke m’dzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+ 34 Pamenepo Aisiraeli ananyamula ufa wokanda wa mkate wopanda chofufumitsa. Anaunyamulira m’zokandiramo ufa pamapewa awo atazikulunga m’nsalu zawo. 35 Ndipo ana a Isiraeli anachita mogwirizana ndi mawu onse amene Mose anawauza, motero anapempha Aiguputo zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala.+ 36 Choncho Yehova anachititsa Aiguputo kukomera mtima anthu ake,+ moti Aiguputo anawapatsa zinthu zonse zimene anapempha,+ ndipo iwo anatenga zinthu zambiri za Aiguputo.+

37 Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Amuna amphamvu oyenda pansi analipo pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ 38 Ndipo khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ anapita limodzi ndi ana a Isiraeli. Anapitanso ndi nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zambirimbiri. 39 Ndiyeno ufa wokanda umene anachoka nawo ku Iguputo uja anayamba kuuphika mikate yozungulira yopanda chofufumitsa, chifukwa ufa wokandawo unalibe zofufumitsa. Ufawo unalibe zofufumitsa chifukwa chakuti anawapitikitsa ku Iguputo ndipo anachoka mofulumira kwambiri. Komanso iwo anaphika mikateyo chifukwa chakuti sanathe kukonza chakudya chilichonse ponyamuka.+

40 Ndiyeno ana a Isiraeli, amene anakhala+ ku Iguputo,+ anakhala m’dziko lachilendo* zaka 430.+ 41 Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinatha, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Iguputo.+ 42 Usiku umenewu ndi wofunika kuukumbukira polemekeza Yehova, chifukwa anawatulutsa m’dziko la Iguputo. Yehova anafuna kuti ana a Isiraeli onse, m’mibadwo yawo yonse, azikumbukira usiku umenewu.+

43 Chotero Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Lamulo la pasika ndi ili:+ Mlendo* asadye nawo.+ 44 Koma mwamuna amene ndi kapolo wogulidwa ndi ndalama, muzim’dula.+ Akadulidwa nayenso angathe kudya. 45 Mlendo wobwera kudzakhala nanu ndiponso waganyu asadye nawo. 46 Muzidyera m’nyumba imodzi. Musatuluke panja ndi nyama iliyonse. Komanso musaphwanye fupa lililonse la nyamayo.+ 47 Khamu lonse la Isiraeli lizichita chikondwerero chimenechi.+ 48 Ngati mlendo wokhala nanu akufuna kuchita nanu chikondwerero cha pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wa m’nyumba yake adulidwe.+ Akatero atha kuchita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo. 49 Lamulo lililonse ligwire ntchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.”+

50 Choncho ana onse a Isiraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aroni. Anachitadi momwemo.+ 51 Ndipo pa tsiku limeneli, Yehova anatulutsa ana a Isiraeli malinga ndi makamu awo+ m’dziko la Iguputo.

13 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Ndipatulireni mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa ana a Isiraeli. Ameneyu ndi wanga.”+

3 Chotero Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lino limene munatuluka mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova anakutulutsani mmenemo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+ 4 Mukutuluka lero m’mwezi wa Abibu.*+ 5 Ndipo Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani,+ pamenepo muzidzachita mwambo uwu m’mwezi uno. 6 Muzidzadya mikate yosafufumitsa masiku 7,+ ndipo pa tsiku la 7 limenelo muzidzachita chikondwerero kwa Yehova.+ 7 Muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa kwa masiku 7.+ Musamadzapezeke ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+ Mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa usamadzapezeke pena paliponse m’dziko lanu.+ 8 Ndiyeno pa tsiku limenelo udzauze mwana wako kuti, ‘Ndikuchita izi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira potuluka mu Iguputo.’+ 9 Chotero mwambo umenewu uzikukumbutsani zimene zinachitikazi ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi pamphumi panu,+ kuti chilamulo cha Yehova chikhale pakamwa panu.+ Zizikhala choncho chifukwa Yehova anakutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ 10 Ndipo muzisunga lamulo ili pa nthawi yake yoikidwiratu chaka ndi chaka.+

11 “Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani,+ monga momwe analumbirira kwa inu ndi kwa makolo anu,+ akadzakupatsani dzikolo, 12 pamenepo muzidzapereka kwa Yehova mwana aliyense woyamba kubadwa,+ ndi mwana aliyense wa ziweto zanu woyamba kubadwa.+ Chachimuna chilichonse n’cha Yehova.+ 13 Mwana aliyense woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa, koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi.+ Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+

14 “Ndiyeno m’tsogolo, mwana wanu akadzakufunsani+ kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mudzamuyankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi mphamvu ya dzanja lake mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo.+ 15 Koma Farao anaumitsa mtima wake posalola kuti ife tichoke,+ motero Yehova anapha mwana woyamba kubadwa aliyense m’dziko la Iguputo,+ kuyambira mwana woyamba kubadwa wa munthu mpaka mwana woyamba kubadwa wa nyama.+ N’chifukwa chake tikupereka nsembe kwa Yehova ana onse a nyama oyamba kubadwa,+ ndipo tikuwombola mwana woyamba kubadwa aliyense mwa ana athu.’+ 16 Mwambo umenewu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi chomanga pamphumi panu,*+ chifukwa Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.”+

17 Farao atalola kuti ana a Isiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse m’dziko la Afilisiti ngakhale kuti kunali kufupi, pakuti Mulungu anati: “Anthu angataye mtima atakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.”+ 18 Chotero Mulungu anachititsa ana a Isiraeli kuyenda njira yaitali yodutsa m’chipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma iwo potuluka m’dziko la Iguputo, anayenda mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ 19 Choncho Mose anatenga mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeli, kuti: “Ndithudi, Mulungu adzakukumbukirani,+ ndipo pochoka kuno mudzatenge mafupa anga.”+ 20 Motero ananyamuka ku Sukoti n’kukamanga msasa ku Etamu m’malire a chipululu.+

21 Yehova anali kuyenda patsogolo pawo mumtambo woima njo ngati chipilala powatsogolera usana,+ ndipo usiku anali kuwatsogolera m’moto woima njo ngati chipilala kuti uziwaunikira, kuti apitirizebe ulendo usana ndi usiku.+ 22 Choncho mtambowo sunachoke patsogolo pa anthuwo usana, ngakhalenso motowo sunachoke usiku.+

14 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti abwerere ndi kumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, koma moyang’anizana ndi Baala-zefoni.+ Mumange msasa wanu pafupi ndi nyanja, patsogolo pa Baala-zefoni. 3 Ndiyeno ponena za ana a Isiraeli, Farao adzati, ‘Asokonezeka ndipo akungoyendayenda m’dziko lathu. Chipululu chawatsekera.’+ 4 Pamenepo ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzapezerapo ulemerero mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi momwemo.

5 Kenako mfumu ya Iguputo inauzidwa kuti Aisiraeli athawa. Pomwepo mtima wa Farao ndi atumiki ake unasinthanso ataganizira za Aisiraeli,+ moti anati: “Tachitanji pamenepa polola akapolo athu Aisiraeli kuchoka?”+ 6 Choncho anakonzekeretsa magaleta* ake ankhondo, n’kutenganso asilikali ake.+ 7 Anatenga magaleta osankhidwa mwapadera 600+ ndi magaleta ena onse a Iguputo, ndipo lililonse la magaletawo munakwera asilikali. 8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake,+ ndipo anathamangira ana a Isiraeli pamene iwo anali kutuluka ndi dzanja lokwezeka.*+ 9 Motero Aiguputo anali kuwathamangira, ndipo magaleta onse a Farao, asilikali apamahatchi+ ndi magulu ake ankhondo anawayandikira. Aisiraeliwo anali atamanga msasa m’mphepete mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti moyang’anizana ndi Baala-zefoni.+

10 Farao atafika pafupi, ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+ 11 Choncho iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere m’chipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi, kutitulutsa mu Iguputo? 12 Kodi si zimene tinakuuza tili ku Iguputo, kuti, ‘Tisiye tizitumikira Aiguputo’? Chifukwa n’kwabwino kutumikira Aiguputo kusiyana n’kuti tifere m’chipululu.”+ 13 Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Chilimikani ndi kuona chipulumutso cha Yehova chimene akuchitireni lero.+ Pakuti Aiguputo amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso, ndithu, simudzawaonanso.+ 14 Yehova adzakumenyerani nkhondo,+ ndipo inu mudzakhala chete, osachitapo kalikonse.”

15 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “N’chifukwa chiyani ukudandaula?+ Uza ana a Isiraeli kuti anyamuke. 16 Ndipo iwe, tenga ndodo yako+ ndi kutambasula dzanja lako kuloza panyanja kuti nyanjayo igawanike.+ Ukatero ana a Isiraeli adutsa pakati pa nyanja, panthaka youma.+ 17 Koma ine ndilola Aiguputo kuumitsa mitima yawo,+ kuti atsatire Aisiraeli panyanjapo, kutinso ndipezerepo ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magulu ake onse ankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+ 18 Ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzipezera ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.”+

19 Ndiyeno mngelo+ wa Mulungu woona amene anali kuyenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka n’kupita kumbuyo kwawo. Motero, mtambo woima njo ngati chipilala uja unachoka kutsogolo n’kukaima kumbuyo kwawo.+ 20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unali kuchititsa mdima, ndipo mbali ina unali kuwaunikira usiku.+ Ndipo gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.

21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+ 22 Patapita nthawi ana a Isiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma,+ madziwo ataima ngati khoma* kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 23 Pamenepo Aiguputo anawalondola, ndipo mahatchi onse a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi, anayamba kuwathamangira,+ kulowa pakati pa nyanja. 24 Ndiyeno pa nthawi ya ulonda wam’mawa,* Yehova ali mumtambo ndi moto woima njo ngati chipilala,+ anayang’ana gulu la Aiguputo, ndipo anachititsa Aiguputowo kusokonezeka.+ 25 Iye anali kugulula mawilo a magaleta awo moti anali kuwayendetsa movutikira.+ Pamenepo Aiguputo anayamba kunena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+

26 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza panyanja,+ kuti madzi abwerere ndi kumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.” 27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza panyanja, ndipo nyanjayo inayamba kubwerera m’malo mwake, kuli pafupi kucha. Pamenepo Aiguputo anayamba kuthawa kuti madziwo asawapeze, koma Yehova anakutumulira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+ 28 Choncho madziwo anabwereradi,+ ndipo anamiza magaleta ankhondo ndi asilikali apamahatchi a magulu onse ankhondo a Farao, amene analondola Aisiraeli m’nyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+

29 Koma ana Aisiraeli anayenda panthaka youma pakati pa nyanja,+ ndipo madzi anaima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 30 Choncho pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa Isiraeli m’manja mwa Aiguputo,+ ndipo Isiraeli anaona Aiguputo atafa m’mphepete mwa nyanja.+ 31 Isiraeli anaonanso dzanja lamphamvu limene Yehova anagonjetsa nalo Aiguputo. Pamenepo Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.+

15 Pa nthawiyo Mose ndi ana a Isiraeli anayamba kuimbira Yehova nyimbo iyi, kuti:+

“Ndiimbira Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa.+

Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.+

 2 Mphamvu ndi nyonga yanga ndi Ya,*+ pakuti wandipulumutsa.+

Ameneyu ndi Mulungu wanga, ndidzam’tamanda.+ Ndiye Mulungu wa atate anga,+ ndidzam’kweza.+

 3 Yehova ndi wankhondo.+ Dzina lake ndi Yehova.+

 4 Magaleta a Farao ndi magulu ake ankhondo wawaponyera m’nyanja.+

Asilikali a Farao osankhidwa mwapadera amizidwa mu Nyanja Yofiira.+

 5 Amizidwa ndi madzi amphamvu.+ Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+

 6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, likusonyeza kupambana kwa mphamvu zake.+

Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.+

 7 Ndipo mu ukulu wanu wopambana mumagwetsa otsutsana nanu.+

Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.+

 8 Ndi mpweya wotuluka m’mphuno mwanu,+ madzi anaunjikika pamodzi.

Madzi oyenda anaima ngati khoma.

Madzi amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.

 9 Mdaniyo anati, ‘Ndiwathamangira,+ ndi kuwapeza!+

Ndigawa chuma chawo.+ Pamenepo moyo wanga ukhutira ndi zimene ndawachita!

Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+

10 Mwapemerera mpweya wanu,+ ndipo nyanja yawamiza.+

Amira ngati mtovu m’madzi akuya.+

11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+

Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+

12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,+ ndipo dziko lawameza.+

13 Mwa kukoma mtima kwanu kosatha, mwatsogolera anthu amene munawawombola.+

Mwa mphamvu yanu, inu mudzatengera anthu anu kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.+

14 Anthu adzamva+ ndipo adzatekeseka.+

Okhala ku Filisitiya adzamva zopweteka ngati za pobereka.+

15 Pamenepo mafumu a ku Edomu adzasokonezeka.

Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera ndi mantha.+

Ndithu, anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+

16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+

Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.

Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,

Kufikira anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+

17 Mudzawabweretsa ndi kuwakhazikitsa m’phiri limene ndi cholowa chanu.+

Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukakhalemo,+ inu Yehova.

Malo opatulika+ amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.

18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale. Adzalamulira mpaka muyaya.+

19 Mahatchi a Farao,+ magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa m’nyanja,+

Yehova wabweza madzi a m’nyanjamo ndi kuwamiza.+

Koma ana a Isiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+

20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, mlongo wake wa Aroni,+ anatenga maseche m’manja mwake,+ ndipo akazi ena onse anam’tsatira akuimba maseche ndi kuvina.+ 21 Ndipo pamene amuna anali kuimba, Miriamu anathirira mang’ombe kuti:+

“Imbirani Yehova+ pakuti wakwezeka koposa.+

Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.”+

22 Kenako Mose anauza Isiraeli kuti anyamuke pa Nyanja Yofiira ndipo analowa m’chipululu cha Shura.+ Iwo anayenda m’chipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.+ 23 Kenako anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Mara.*+ 24 Pamenepo anthu anayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose,+ kuti: “Timwa chiyani?” 25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anam’sonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko m’madzi moti madziwo anakhala okoma.+

Pamenepo Mulungu anawakhazikitsira lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo pa nthawiyo anawayesa.+ 26 Ndiyeno anawauza kuti: “Ngati mudzamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani miliri iliyonse imene ndinagwetsera Iguputo,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikukuchiritsani.”+

27 Kenako anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza.+ Iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.

16 Kenako ananyamuka ku Elimu,+ ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiwiri atachoka m’dziko la Iguputo, khamu lonse la ana a Isiraeli linafika kuchipululu cha Sini,+ chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.

2 M’chipululumo khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzira Mose ndi Aroni.+ 3 Ndipo ana a Isiraeli anali kunena kwa Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera+ m’dziko la Iguputo, kumene tinali kudya nyama+ ndipo tinali kudya mkate ndi kukhuta. M’malomwake mwatibweretsa m’chipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+

4 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Ndikuvumbitsirani mkate kuchokera kumwamba,+ ndipo anthu azipita kukatola. Aliyense azitola muyezo wom’kwanira pa tsikulo.+ Ndikuchita izi kuti ndiwayese ngati adzatsatira chilamulo changa kapena ayi.+ 5 Pa tsiku la 6+ azikonzeratu zimene atola, ndipo muyezo wake uzikhala wowirikiza kawiri zimene amatola tsiku ndi tsiku.”+

6 Choncho Mose ndi Aroni anauza ana onse a Isiraeli kuti: “Madzulo ano mudziwa kuti Yehova ndiye anakutulutsani m’dziko la Iguputo.+ 7 Ndipo m’mawa mudzaona ulemerero wa Yehova+ chifukwa wamva kung’ung’udza kwanu kotsutsana ndi Yehovayo. Ife ndife ndani kuti muziting’ung’udzira?” 8 Ndiyeno Mose anapitiriza kuti: “Mudzaona zimenezi Yehova akakupatsani nyama yoti mudye madzulo ano, ndi mkate wokwanira m’mawa, chifukwa Yehova wamva kung’ung’udza kwanu kumene mukum’ng’ung’udzira. Ife ndife ndani? Kung’ung’udza kwanu si kotsutsana ndi ife, koma n’kotsutsana ndi Yehova.”+

9 Chotero Mose anauza Aroni kuti: “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova, chifukwa wamva kung’ung’udza kwanu.’”+ 10 Ndiyeno Aroni atangomaliza kulankhula ndi khamu lonse la ana a Isiraeli, iwo anatembenuka ndi kuyang’ana kuchipululu. Ndipo taonani! Ulemerero wa Yehova unaonekera mumtambo.+

11 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 12 “Ndamva kung’ung’udza kwa ana a Isiraeli.+ Auze kuti, ‘Madzulo kuli kachisisira* mudzadya nyama, ndipo m’mawa mudzadya mkate ndi kukhuta.+ Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+

13 Choncho zinachitikadi kuti madzulo kunabwera zinziri+ zimene zinakuta msasa wonse, ndipo m’mawa kunachita mame kuzungulira msasa wonsewo.+ 14 Kenako mame aja anauma ndipo panthaka ya m’chipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba+ koma tosalala ngati mame+ amene aundana panthaka. 15 Ana a Isiraeli ataona tinthu timeneti anayamba kufunsana kuti: “N’chiyani ichi?” Chifukwa sanadziwe kuti chinali chiyani. Pamenepo Mose anawauza kuti: “Ndi chakudya chimene Yehova wakupatsani.+ 16 Yehova walamula kuti, ‘Tolani chakudya chimenecho, aliyense malinga ndi mmene amadyera.+ Muzitola malinga ndi chiwerengero cha anthu amene ali m’hema wanu. Munthu aliyense muzim’tolera muyezo wa omeri* limodzi.’” 17 Choncho ana a Isiraeli anayamba kuchita zomwezo. Anayamba kutola chakudyacho, moti ena anatola chambiri koma ena chochepa. 18 Akayeza chakudyacho pamuyezo wa omeri, munthu amene anatola chambiri sichinali kuposa muyezowo, ndipo amene anatola chochepa sichinali kuperewera.+ Aliyense anatola malinga ndi mmene amadyera.

19 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Aliyense asasiyeko chakudyachi mpaka m’mawa.”+ 20 Koma iwo sanamvere Mose. Pamene anthu ena anasiyako chakudyacho mpaka m’mawa, chinatuluka mphutsi ndi kununkha,+ moti Mose anawakalipira kwambiri.+ 21 Ndipo m’mawa uliwonse+ anali kukatola chakudyacho, aliyense malinga ndi mmene amadyera. Dzuwa likatentha, chinali kusungunuka.

22 Pa tsiku la 6, anthuwo anatola muyezo wowirikiza kawiri,+ munthu aliyense maomeri awiri. Pamenepo atsogoleri onse a khamu la Isiraeli anabwera kwa Mose kudzanena. 23 Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa tisunga sabata, sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali ndi kuzisunga mpaka m’mawa.” 24 Choncho anasungadi chakudyacho mpaka m’mawa monga momwe Mose anawalamulira, ndipo sichinanunkhe kapena kuchita mphutsi.+ 25 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Idyani chakudyachi lero, chifukwa lero ndi sabata+ la Yehova ndipo simukachipeza kunja kwa msasa. 26 Muzitola chakudyachi masiku 6, koma tsiku la 7 ndi sabata.+ Pa tsiku limeneli sichidzapezeka kunja kwa msasa.” 27 Komabe, pa tsiku la 7 anthu ena anapita kuti akatole chakudyacho, koma sanachipeze.

28 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Kodi anthu inu mudzakanabe kusunga malamulo ndi malangizo anga kufikira liti?+ 29 Dziwani kuti Yehova wakupatsani sabata.+ N’chifukwa chake akukupatsani mkate wa masiku awiri pa tsiku la 6. Pa tsiku la 7 aliyense azikhala pamalo ake.+ Munthu asachoke pamalo ake.” 30 Ndipo anthu anasunga sabata tsiku la 7.+

31 Chotero nyumba ya Isiraeli inayamba kutcha chakudyacho kuti “mana.”* Chinali choyera ngati njere ya mapira,* ndipo kukoma kwake kunali ngati makeke opyapyala othira uchi.+ 32 Pamenepo Mose anati: “Yehova walamula kuti, ‘Dzazani muyezo umodzi wa omeri ndi mana kuti asungidwe m’mibadwo yanu yonse,+ n’cholinga choti adzaone mkate umene ndinakudyetsani m’chipululu pamene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.’”+ 33 Ndiyeno Mose anauza Aroni kuti: “Tenga mtsuko ndi kuthiramo mana muyezo umodzi wa omeri ndi kuuika pamaso pa Yehova kuti asungidwe m’mibadwo yanu yonse.”+ 34 Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aroni anaikadi mtsukowo patsogolo pa Umboni*+ kuti manawo asungidwe. 35 Ndipo ana a Isiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa m’dziko lokhalidwa ndi anthu.+ Mana ndiwo anali chakudya chawo mpaka pamene anafika m’malire a dziko la Kanani.+ 36 Tsopano miyezo 10 ya omeri inali kukwana muyezo umodzi wa efa.*

17 Ndipo khamu lonse la ana a Isiraeli linanyamuka kuchipululu cha Sini.+ Ulendowo anaugawa mitundamitunda, malinga ndi mmene Yehova anawauzira,+ ndipo anamanga msasa wawo pa Refidimu.+ Koma pamenepo panalibe madzi akumwa.

2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose kuti:+ “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+ 3 Choncho anthu anamva ludzu pamenepo, ndipo anthuwo anapitiriza kung’ung’udzira Mose kuti: “N’chifukwa chiyani unatitulutsa mu Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu, ifeyo pamodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”+ 4 Chotero Mose anafuulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!”+

5 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Yenda kutsogolo kwa anthu+ ndipo utenge ena mwa akulu a Isiraeli komanso ndodo yako imene unamenya nayo mtsinje wa Nailo.+ Uitenge m’dzanja lako ndipo uziyenda. 6 Tamvera! Ine ndidzatsogola kukaima pathanthwe ku Horebe.* Kumeneko ukamenye thanthwelo, ndipo padzatuluka madzi amene anthu adzamwa.”+ Chotero Mose anachitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli, 7 ndipo iye anatcha malowo Masa*+ ndi Meriba,*+ chifukwa ana a Isiraeli anakangana ndi Mose, komanso chifukwa cha kuyesa Yehova+ kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?”+

8 Ndiyeno Aamaleki+ anabwera kudzamenyana ndi Isiraeli ku Refidimu.+ 9 Zitatero Mose anauza Yoswa* kuti:+ “Tisankhire amuna, ndipo upite nawo+ kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona m’dzanja langa.”+ 10 Yoswa anachitadi zimene Mose anamuuza,+ kuti amenyane ndi Aamaleki. Mose, Aroni ndi Hura+ anapita pamwamba pa phiri.

11 Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, Mose akangokweza dzanja lake m’mwamba, Aisiraeli anali kupambana pankhondoyo,+ koma akangotsitsa dzanja lake, Aamaleki anali kupambana. 12 Manja a Mose atatopa, anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo. Aroni ndi Hura anachirikiza manja ake, wina mbali ina winanso mbali ina, moti manja ake anakhalabe choncho mpaka dzuwa kulowa. 13 Motero ndi lupanga, Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yawo.+

14 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Lemba zimenezi m’buku monga chikumbutso+ ndi kumuuza Yoswa kuti, ‘M’kupita kwa nthawi ndidzafafaniziratu Aamaleki padziko lapansi* ndipo sadzakumbukika n’komwe.’”+ 15 Pamenepo Mose anamanga guwa lansembe n’kulitcha kuti Yehova-nisi,* 16 ndipo anati: “Popeza dzanja laukira mpando wachifumu+ wa Ya,+ Yehova adzamenya nkhondo ndi Aamaleki ku mibadwomibadwo.”+

18 Tsopano Yetero, wansembe wa ku Midiyani, apongozi ake a Mose,+ anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi Aisiraeli, anthu a Mulungu, ndi mmene Yehova anawatulutsira ku Iguputo.+ 2 Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anatenga Zipora, mkazi wa Mose, amene Mose anali atamutumiza kwawo, 3 ndipo anatenganso ana aamuna awiri+ a Zipora. Mwana wina, Mose anamutcha dzina lakuti Gerisomu,*+ ndipo anati: “Chifukwa ndine mlendo m’dziko lino.” 4 Ndipo mwana winayo anamutcha Eliezere,*+ ndipo anati: “Mulungu wa atate anga ndiye mthandizi wanga, pakuti anandipulumutsa kulupanga la Farao.”+

5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, pamodzi ndi ana a Mose awiri aamuna ndi mkazi wake, anapita kwa Mose kuchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+ 6 Ndiyeno anatumiza mawu kwa Mose, kuti: “Ine Yetero, mpongozi wako,+ ndafika pamodzi ndi mkazi wako ndi ana ako awiri.” 7 Nthawi yomweyo Mose anatuluka kukachingamira apongozi ake, ndipo anagwada n’kuwaweramira, kenako n’kuwapsompsona.+ Pamenepo anayamba kulonjerana ndi kufunsana za moyo. Kenako anapita kukalowa m’hema.

8 Motero Mose anawafotokozera apongozi akewo zonse zimene Yehova anachitira Farao ndi Iguputo chifukwa cha Isiraeli.+ Anawafotokozeranso mavuto onse amene anakumana nawo m’njira,+ ndi mmene Yehova anali kuwalanditsira.+ 9 Yetero anasangalala kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli powalanditsa m’manja mwa Aiguputo.+ 10 Choncho Yetero anati: “Yehova adalitsike, iye amene anakulanditsani m’manja mwa Aiguputo ndiponso m’dzanja la Farao, amenenso analanditsa anthuwa m’manja mwa Aiguputo.+ 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndiye wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ Zimenezi zinaoneka Aiguputo atasonyeza kudzikuza pamaso pa Aisiraeli.” 12 Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anabweretsa* nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu.+ Ndipo Aroni ndi akulu onse a Isiraeli anabwera n’kudyera limodzi mkate ndi apongozi ake a Mose, pamaso pa Mulungu woona.+

13 Pa tsiku lotsatira, Mose anakhala pansi monga mwa masiku onse kuti atumikire anthu monga woweruza,+ ndipo anthu anali kubwera ndi kuimirira pamaso pa Mose kuyambira m’mawa mpaka madzulo. 14 Pamenepo apongozi a Mose anaona zonse zimene iye anali kuchitira anthuwo. Ndiyeno anati: “Kodi anthuwa ukuchita nawo chiyani? N’chifukwa chiyani wangokhala wekha kupereka ziweruzo ndipo anthu onse ali chiimire pamaso pako kuyambira m’mawa mpaka madzulo?” 15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa amabwera kwa ine kuti adzamve ziweruzo za Mulungu.+ 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo+ ayenera kubwera nawo kwa ine, ndipo ndiyenera kuwaweruza ndi kuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+

17 Pamenepo apongozi a Mose anamuuza kuti: “Imene ukutsatirayi si njira yabwino. 18 Ndithu mutopa nazo zimenezi, iwe ndi anthu amene uli nawowa, chifukwa ntchito imeneyi yakukulira kwambiri.+ Sungathe kuichita wekha.+ 19 Tsopano mvera zimene ndikufuna kukuuza.+ Ndikulangiza ndipo Mulungu adzakhala nawe.+ Iwe ukhale woimira anthuwa kwa Mulungu woona,+ ndipo ndiwe amene uzipititsa milandu kwa Mulungu woona.+ 20 Ndipo uziwaphunzitsa za malangizo ndi malamulo,+ ndi kuwauza njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.+ 21 Koma mwa anthu onsewa, usankhe amuna oyenerera,+ oopa Mulungu,+ okhulupirika,+ odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kukhala otsogolera anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22 Amenewa ndiwo aziweruza anthu pa nkhani iliyonse yoyenera. Ndiyeno pakakhala nkhani iliyonse yaikulu azibwera nayo kwa iwe,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza aziisamalira. Choncho amunawo athandizane nawe kunyamula mtolowu, kuti udzipeputsire ntchito.+ 23 Ukachita zimenezi, ndipo izi n’zimene Mulungu wakulamula kuchita, pamenepo udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kumahema awo mu mtendere.”+

24 Nthawi yomweyo Mose anamvera zimene apongozi ake anamuuza ndipo anachita zonse zimene ananena.+ 25 Ndipo Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli yense ndi kuwapatsa udindo wokhala atsogoleri a anthu,+ kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26 Motero iwo anali kuweruza anthuwo pa nkhani iliyonse yoyenera. Nkhani yovuta anali kupita nayo kwa Mose,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza anali kuisamalira. 27 Kenako Mose anaperekeza apongozi ake+ ndi kutsanzikana nawo, ndipo iwo anabwerera kwawo.

19 M’mwezi wachitatu kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ pa tsiku lomwelo,* iwo analowa m’chipululu cha Sinai.+ 2 Ananyamuka ku Refidimu+ n’kulowa m’chipululu cha Sinai+ ndi kumanga msasa wawo m’chipululumo. Aisiraeli anamanga msasawo pafupi ndi phiri la Sinai.+

3 Pamenepo Mose anakwera m’phirimo kukaonekera kwa Mulungu woona. Ndipo Yehova anayamba kumulankhula m’phirimo+ kuti: “Ukanene mawu awa kunyumba ya Yakobo, ana a Isiraeli kuti, 4 ‘Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo,+ kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga ndi kukubweretsani kwa ine.+ 5 Tsopano ngati mudzalabadiradi+ mawu anga ndi kusunga pangano langa,+ pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+ 6 Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa ana a Isiraeli.”

7 Choncho Mose anatsika n’kuitanitsa akulu onse+ a anthu, ndipo anawauza mawu onse amene Yehova anam’lamula.+ 8 Kenako anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.”+ Nthawi yomweyo Mose anatenga mawu a anthuwo ndi kubwerera nawo kwa Yehova.+ 9 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Tamvera! Nditsikira kwa iwe mumtambo wakuda,+ kuti anthu amve pamene ndikulankhula ndi iwe,+ ndi kuti iwenso azikukhulupirira nthawi zonse.”+ Choncho Mose anali atanena mawu a anthuwo kwa Yehova.

10 Ndipo Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa anthu, uwayeretse lero ndi mawa, ndipo achape zovala zawo.+ 11 Pa tsiku lachitatu akhale okonzeka, chifukwa pa tsiku lachitatulo Yehova adzatsikira paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.+ 12 Ndipo anthuwo uwadulire malire kuzungulira phiri lonse, ndi kuwauza kuti, ‘Onetsetsani kuti musakwere m’phiri, ndipo musakhudze tsinde lake. Aliyense amene adzakhudza phirili adzaphedwa ndithu.+ 13 Palibe munthu amene ayenera kudzakhudza wolakwayo, chifukwa adzaponyedwa miyala kapena kulasidwa ndithu. Kaya ndi nyama kapena munthu, sadzayenera kukhala ndi moyo.’+ Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira,+ anthu onse ayandikire kuphiri.”

14 Ndiyeno Mose anatsika m’phirimo kupita kwa anthu n’kuyamba kuyeretsa anthuwo. Ndipo iwo anayamba kuchapa zovala zawo.+ 15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Pofika tsiku lachitatu mukhale okonzeka.+ Amunanu musayandikire akazi anu.”*+

16 Pa tsiku lachitatu kutacha, kunayamba kuchita mabingu ndi mphezi.+ Mtambo wakuda+ unakuta phiri, ndipo kunamveka kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa,+ moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+ 17 Zitatero Mose anatulutsa anthuwo mumsasa kuti akakumane ndi Mulungu woona, ndipo anapita kukaima m’tsinde mwa phirilo.+ 18 Pamenepo phiri la Sinai linafuka utsi ponseponse,+ chifukwa chakuti Yehova anatsikira paphiripo m’moto.+ Utsi wakewo unali kukwera kumwamba ngati utsi wa uvuni,+ ndipo phiri lonse linali kunjenjemera kwambiri.+ 19 Pamene kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kunali kupitiriza kukwererakwerera, Mose anayamba kulankhula, ndipo Mulungu woona anamuyankha ndi mawu amphamvu.+

20 Pamenepo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamwamba pa phirilo. Kenako Yehova anaitana Mose kuti akwere pamwamba pa phirilo, ndipo Mose anakweradi.+ 21 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tsika ukachenjeze anthuwo, kuti asayese kudumpha malire kufika kwa Yehova pofuna kuonetsetsa, chifukwa onse oterowo angafe.+ 22 Nawonso ansembe amene amayandikira kwa Yehova kawirikawiri adziyeretse,+ kuti mkwiyo wa Yehova usawayakire.”+ 23 Pamenepo Mose anauza Yehova kuti: “Anthuwa sangafike paphiri la Sinai, chifukwa inu munawachenjeza kale pamene munandiuza kuti: ‘Udule malire kuzungulira phiri kuti likhale lopatulika.’”+ 24 Koma Yehova anamuuza kuti: “Pita, tsika, ndipo ukabwerenso iweyo limodzi ndi Aroni. Koma ansembe ndiponso anthu asalumphe malire kuti akwere kwa Yehova, chifukwa mkwiyo wake ungawayakire.”+ 25 Mose anachitadi zomwezo, ndipo anatsikira kwa anthu n’kuwauza zonsezi.+

20 Ndipo Mulungu anayamba kulankhula mawu awa, kuti:+

2 “Ine ndine Yehova Mulungu wako,+ amene ndinakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 3 Usakhale ndi milungu ina iliyonse+ kupatulapo ine.*

4 “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi.*+ 5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+ 6 Koma ndimasonyeza kukoma mtima kosatha ku mibadwo masauzande chifukwa cha anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.+

7 “Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+

8 “Pokumbukira kuti muyenera kusunga tsiku la sabata ndi kuliona kukhala lopatulika,+ 9 muzichita ntchito zanu zonse masiku 6.+ 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+ 11 Pakuti m’masiku 6 Yehova anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili mmenemo,+ ndipo anayamba kupuma pa tsiku la 7.+ N’chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la sabata ndi kulipanga kukhala lopatulika.+

12 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+

13 “Usaphe munthu.*+

14 “Usachite chigololo.+

15 “Usabe.+

16 “Usapereke umboni wonamizira mnzako.+

17 “Usalakelake nyumba ya mnzako. Usalakelake mkazi wa mnzako,+ kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake, bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”+

18 Ndiyeno anthu onse anali kumva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anali kuona kung’anima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva ndi kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaimabe patali.+ 19 Ndipo anthuwo anauza Mose kuti: “Iweyo uzilankhula ndi ife, ndipo ife tizimvetsera, koma Mulungu asalankhule ndi ife kuopera kuti tingafe.”+ 20 Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: “Musaope, chifukwa Mulungu woona wabwera+ kuti akuyeseni, ndi kuti mupitirizebe kumuopa kuti musachimwe.”+ 21 Choncho anthuwo anaimabe patali pomwepo, koma Mose anayandikira mtambo wakuda uja kumene kunali Mulungu woona.+

22 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+ “Ana a Isiraeli uwauze kuti, ‘Mwadzionera nokha kuti ine ndalankhula nanu kuchokera kumwamba.+ 23 Musadzipangire milungu yasiliva ndi milungu yagolide kuti muziipembedza pamodzi ndi ine.+ 24 Mundipangire guwa lansembe ladothi,+ ndipo muziperekapo nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano,* nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu.+ M’malo onse amene ndidzachititsa dzina langa kukumbukika ndidzabwera kwa inu ndipo ndidzakudalitsani ndithu.+ 25 Mukandipangira guwa lansembe lamiyala, musamangire miyala yosema. Mukangosema mwala wa guwalo, ndiye kuti mwaipitsa chinthu chopatulika.+ 26 Ndipo guwa langa lansembe lisakhale la masitepe, kuti pokwera pamenepo maliseche anu angaonekere.’

21 “Ndipo izi ndizo zigamulo zoti uwaikire:+

2 “Ukagula kapolo wachiheberi,+ adzakhala kapolo wako kwa zaka 6, koma m’chaka cha 7 azimasuka ndipo azichoka osam’lipiritsa.+ 3 Ngati anabwera ali yekha, adzachokanso ali yekha. Ngati ali ndi mkazi, mkazi wakeyo adzapita naye. 4 Ngati mbuye wake wamupatsa mkazi n’kubereka naye ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo ndi ana ake adzakhala a mbuye wake,+ ndipo mwamunayo adzachoka yekha.+ 5 Koma kapoloyo akanena motsimikiza kuti, ‘Ndimam’konda kwambiri mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana anga, ndipo sindikufuna kuchoka monga womasulidwa,’+ 6 pamenepo mbuye wakeyo azibwera naye pafupi ndi Mulungu woona ndi kufika naye pachitseko kapena pafelemu. Akatero mbuye wakeyo amuboole khutu ndi choboolera, ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.+

7 “Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi kukhala kapolo,+ sadzachoka mmene akapolo aamuna amachokera. 8 Ngati mbuye wake sanakondwere naye kuti akhale mkazi wake wamng’ono+ koma wamulola kuwomboledwa, mbuyeyo alibe ufulu womugulitsa kwa anthu a mtundu wina chifukwa wam’chitira zachinyengo. 9 Koma akamupereka kwa mwana wake wamwamuna, azim’patsa ufulu wonse umene umaperekedwa kwa ana aakazi.+ 10 Mwana wamwamunayo akakwatira mkazi wina, woyambayo asaleke kum’patsa chakudya, zovala+ ndi mangawa ake+ a mu ukwati. 11 Koma ngati sakum’patsa zinthu zitatu zimenezi, mkaziyo achoke popanda kupereka chilichonse, popanda kumulipiritsa ndalama.

12 “Amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa ndithu.+ 13 Koma ngati sanachite kum’dikirira, ndipo Mulungu woona walola kuti mwangozi munthuyo afere m’manja mwake,+ pamenepo ndidzakukonzerani malo amene angathawireko.+ 14 Munthu amene wapsera mtima mnzake mpaka kumupha mwachiwembu,+ ngakhale atathawira kuguwa langa lansembe kuti atetezeke, muzimuchotsa n’kukamupha.+ 15 Womenya abambo ake ndi mayi ake aziphedwa ndithu.+

16 “Wakuba munthu+ ndi kum’gulitsa+ kapena munthu amene wapezeka ndi munthu wobedwayo, aziphedwa ndithu.+

17 “Wotemberera bambo ake ndi mayi ake aziphedwa ndithu.+

18 “Anthu akayamba kukangana, wina n’kutema mnzake ndi mwala kapena khasu, mnzakeyo osafa koma wadwala ndipo wagona, 19 akadzuka n’kuyamba kuyendayenda kunja pogwiritsa ntchito ndodo, pamenepo amene anam’tema uja salandira chilango. Koma adzapereka malipiro a nthawi imene wotemedwayo wakhala wosagwira ntchito, mpaka mnzakeyo atachiriratu.

20 “Munthu akamenya+ kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, kapoloyo n’kumufera, munthuyo azilangidwa ndithu.+ 21 Koma ngati kapoloyo wakhalabe ndi moyo tsiku limodzi kapena masiku awiri, mbuye wakeyo sayenera kulangidwa chifukwa kapoloyo ndi chuma chake.

22 “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati moti mkaziyo n’kubereka mwana+ koma palibe amene wamwalira, wovulaza mkaziyo azimulipiritsa ndithu malinga ndi zimene mwiniwake wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera mwa oweruza.+ 23 Ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.+ 24 Koma wina akavulaza mnzake koopsa, pazikhala diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi,+ 25 kutentha ndi moto kulipira kutentha ndi moto, chilonda kulipira chilonda, kumenya kulipira kumenya.+

26 “Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena kapolo wake wamkazi padiso n’kumuvulaza kwambiri, azimasula kapoloyo ndi kumulola kuchoka monga malipiro a diso lake.+ 27 Ndipo akagulula dzino la kapolo wake wamwamuna kapena la kapolo wake wamkazi, azimasula kapoloyo ndi kumulola kuchoka monga malipiro a dzino lake.

28 “Ng’ombe ikagunda mwamuna kapena mkazi, munthuyo n’kumwalira, ng’ombeyo iziponyedwa miyala ndi kuphedwa+ ndithu, ndipo nyama yake isadyedwe. Zikatero mwiniwake wa ng’ombeyo sayenera kulangidwa. 29 Koma ngati ng’ombe inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwiniwake anachenjezedwapo koma sanali kuiyang’anira, ndiyeno yapha mwamuna kapena mkazi, ng’ombeyo iziponyedwa miyala ndipo mwiniwakeyo aziphedwanso. 30 Ngati waweruzidwa kuti apereke dipo,* ayenera kulipira mtengo wonse wowombolera moyo wake umene amugamula.+ 31 Kaya ng’ombeyo inagunda mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi, mwiniwake aziweruzidwa malinga ndi chigamulo chimenechi.+ 32 Ngati yagunda kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwiniwake azilipira ndalama zokwana masekeli* 30+ kwa mbuye wa kapoloyo, ndipo ng’ombeyo iziponyedwa miyala.

33 “Munthu akasiya dzenje losavindikira, kapena akakumba dzenje koma osatsekapo, ndipo ng’ombe kapena bulu n’kugweramo,+ 34 mwiniwake wa dzenjelo azilipira.+ Malipirowo azipereka kwa mwiniwake wa ng’ombeyo, koma iye azitenga nyama yakufayo. 35 Ng’ombe ya munthu ikavulaza ndi kupha ng’ombe ya mnzake, pamenepo azigulitsa ng’ombe yamoyoyo ndi kugawana ndalamazo, ndipo azigawananso yakufayo.+ 36 Kapena ngati ng’ombe inali kudziwika ndi chizolowezi chogunda zinzake, koma mwiniwake sanali kuiyang’anira,+ azipereka ndithu+ ng’ombe kulipira ng’ombe, ndipo azitenga yakufayo.

22 “Munthu akaba ng’ombe kapena nkhosa, n’kuipha kapena kuigulitsa, azilipira ng’ombe zisanu pa ng’ombe imodzi imene waba, ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi imene waba.+

2 (“Wakuba+ akapezeka akuthyola nyumba kuti abe+ ndipo akakanthidwa n’kufa, amene wamuphayo alibe mlandu wa magazi.+ 3 Ngati dzuwa linali litatuluka, amene wamuphayo ali ndi mlandu wa magazi.)

“Wakuba azilipira ndithu. Ngati alibe kalikonse, pamenepo azigulitsidwa kuti alipire zinthu zimene anabazo.+ 4 Ngati zimene anabazo zapezeka ndi iyeyo zili zamoyo, kaya ndi ng’ombe, bulu kapena nkhosa, azilipira zowirikiza kawiri.

5 “Munthu akalekerera ziweto zake kukadya m’munda wa mpesa kapena wa mbewu zina, kapena watumiza nyama zake zonyamula katundu kukadya m’munda wa munthu wina, azilipira+ popereka zokolola zabwino koposa za m’munda wake wa mpesa kapena za m’munda wake wa mbewu zina.

6 “Moto ukabuka n’kugwirira zomera zaminga, ndipo wafalikira m’munda n’kutentha mitolo yambewu, mbewu zosadula kapena munda wonse,+ amene anayatsa motowo azilipira ndithu chifukwa cha zotenthedwazo.

7 “Munthu akapatsa mnzake ndalama kapena katundu wina kuti amusungire,+ zinthuzo n’kubedwa m’nyumba ya mnzakeyo, wakubayo akapezeka azilipira zowirikiza kawiri.+ 8 Ngati wakubayo sanapezeke, azibweretsa mwininyumbayo pafupi ndi Mulungu woona*+ pofuna kuona ngati iyeyo sanatenge katundu wa mnzakeyo. 9 Koma pa milandu iliyonse+ yokhudza ng’ombe, bulu, nkhosa, chovala, kapena chilichonse chimene chinasowa chimene angachiloze kuti, ‘Ichi n’changa!’ awiri onsewo mlandu wawo uzifika pamaso pa Mulungu woona.+ Amene Mulungu adzamuweruze kuti ndiye woipa, azilipira mnzake zowirikiza kawiri.+

10 “Munthu akapatsa mnzake bulu, ng’ombe, nkhosa kapena chiweto chilichonse kuti amusungire, ndipo chafa, chalumala kapena chabedwa popanda woona zimene zachitika, 11 iye alumbire+ kwa mnzake pamaso pa Yehova kuti si iye amene wachita zimenezo pa katundu wa mnzake.+ Mwini wa katunduyo azivomereza lumbirolo ndipo mnzakeyo asalipire. 12 Koma ngati anachita kum’bera,* azilipira kwa mwini wa katunduyo.+ 13 Ngati nyamayo inaphedwa ndi chilombo,+ azibweretsa nyama yakufayo monga umboni.+ Asalipire pa nyama iliyonse yophedwa ndi chilombo.

14 “Koma ngati munthu wabwereka chiweto kwa mnzake+ ndipo chalumala kapena chafa mwiniwake palibe, wobwerekayo azilipira ndithu.+ 15 Ngati mwiniwake alipo, wobwerekayo asalipire. Ngati anafunika kupereka ndalama kuti abwereke, adzangopereka ndalama yobwerekera chiwetocho.

16 “Mwamuna akanyengerera namwali wosalonjezedwa kukwatiwa n’kugona naye,+ azim’tenga ndithu kukhala mkazi wake atapereka chiwongo.*+ 17 Bambo a namwaliyo akakaniratu kum’patsa mwana wawo, iye aziperekabe chiwongo chimene amaperekera namwali.+

18 “Mkazi wamatsenga musam’lole kukhala ndi moyo.+

19 “Aliyense wogonana ndi nyama aziphedwa ndithu.+

20 “Wopereka nsembe kwa milungu ina osati kwa Yehova yekha aziphedwa ndithu.+

21 “Musachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kum’pondereza,+ chifukwa anthu inu munalinso alendo m’dziko la Iguputo.+

22 “Anthu inu musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye* aliyense.+ 23 Mukamuzunza ngakhale pang’ono, iye n’kundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.+ 24 Pamenepo mkwiyo wanga udzakuyakirani,+ ndipo ndidzakuphani ndithu ndi lupanga, kuti akazi anu akhale akazi amasiye ndiponso ana anu akhale ana amasiye.+

25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+

26 “Mnzako ukamulanda chovala chake monga chikole,+ uzim’bwezera dzuwa likamalowa. 27 Pakuti chofunda chake n’chomwecho.+ Imeneyo ndi nsalu yake yakunja. Adzafunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamumvera ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+

28 “Usatemberere Mulungu+ kapena kutemberera mtsogoleri amene ali pakati pa anthu ako.+

29 “Popereka zokolola zako zambirizo komanso zotuluka moponderamo mphesa ndi moyengeramo mafuta zochulukazo, usapereke monyinyirika.+ Mwana wako wamwamuna woyamba kubadwa uzim’pereka kwa ine.+ 30 Zimene uzichita ndi mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe ndi wa nkhosa yako ndi izi:+ Azikhala ndi mayi wake masiku 7.+ Pa tsiku la 8 uzim’pereka kwa ine.

31 “Inuyo muzikhala anthu oyera pamaso panga+ ndipo musadye nyama imene yaphedwa ndi chilombo kuthengo.+ Imeneyo muziponyera agalu.+

23 “Usafalitse nkhani yabodza.+ Usagwirizane ndi munthu woipa mwa kukhala mboni yokonzera wina zoipa.+ 2 Usatsatire khamu pochita zoipa.+ Pa mlandu usapereke umboni wopotoza chilungamo potsatira khamu la anthu.+ 3 Usakondere munthu wosauka pa mlandu wake.+

4 “Ukapeza ng’ombe kapena bulu wa mdani wako atasochera, um’bweze ndithu kwa mwiniwake.+ 5 Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+

6 “Usapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+

7 “Utalikirane ndi mawu onama.+ Usaphe munthu wosalakwa ndi munthu wolungama, chifukwa woipa sindidzamuyesa wolungama.+

8 “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+

9 “Usapondereze mlendo wokhala pakati panu,+ popeza mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+

10 “Kwa zaka 6 uzilima munda wako ndi kukolola.+ 11 Koma chaka cha 7 usaulime, uusiye kuti ugonere.+ Osauka mwa anthu ako adye za m’mundamo ndipo zimene iwo asiya, zilombo zakutchire zidye.+ Uzichita zimenezi ndi munda wako wa mpesa ndi wa maolivi.

12 “Uzigwira ntchito masiku 6.+ Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma, ndipo mwana wa kapolo wako wamkazi ndi mlendo azipumula.+

13 “Muzisamalira zonse zimene ndakuuzani,+ ndipo musatchule dzina la milungu ina. Lisamveke pakamwa panu.+

14 “Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15 Muzichita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa+ masiku 7 pa nthawi yake m’mwezi wa Abibu,*+ monga momwe ndakulamulirani, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi umenewu. Ndipo palibe ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+ 16 Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+ 17 Katatu pa chaka mwamuna aliyense pakati panu azionekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+

18 “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Ndipo mafuta a chikondwerero changa asamagone mpaka m’mawa.+

19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

20 “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+ 21 Samala ndipo umvere mawu ake. Usam’pandukire, chifukwa sadzalekerera zolakwa zanu,+ pakuti dzina langa lili mwa iye. 22 Koma ukalabadiradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanena,+ pamenepo ndidzalusira adani ako ndi kuvutitsa okuvutitsa.+ 23 Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+ 24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ 25 Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndipo ndidzachotsa matenda pakati panu.+ 26 M’dziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku anu.+

27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+ 28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+ 29 Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+ 30 Ndidzawathamangitsa pamaso pako pang’onopang’ono kufikira mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+

31 “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+ 32 Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33 Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+

24 Choncho Mulungu anauza Mose kuti: “Kwera upite kwa Yehova, iweyo, Aroni, Nadabu, Abihu+ ndi akulu 70+ a Isiraeli, ndipo mugwade chapatali. 2 Mose yekha ayandikire kwa Yehova, koma enawo asayandikire. Anthu ena onse asakwere m’phiri.”+

3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu ndi kuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Pamenepo anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+ 4 Choncho Mose analemba mawu onse a Yehova.+ Ndiyeno anadzuka m’mawa kwambiri n’kumanga guwa lansembe ndi zipilala 12 zoimira mafuko 12 a Isiraeli, m’tsinde mwa phiri.+ 5 Kenako anatuma anyamata a Isiraeli ndipo anyamatawo anapereka nsembe zopsereza komanso anapereka ng’ombe kuti zikhale nsembe zachiyanjano+ kwa Yehova. 6 Pamenepo Mose anatenga hafu ya magazi ndi kuwaika m’mbale zolowa,+ ndipo hafu inayo anawaza paguwa lansembe.+ 7 Ndiyeno anatenga buku la pangano+ ndi kuwerengera anthuwo kuti amve.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+ 8 Pamenepo Mose anatenga magaziwo ndi kuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano+ limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.”

9 Choncho Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera m’phirimo, 10 ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake panali chinthu chooneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, choyera ngati kumwamba.+ 11 Mulungu sanawononge atsogoleri amenewo a ana a Isiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona+ ndipo anadya ndi kumwa.+

12 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Kwera m’phiri muno ufike kwa ine ndi kukhala momwe muno, pakuti ndikufuna kukupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+ 13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka, ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu woona.+ 14 Koma Mose anali atauza akuluwo kuti: “Tidikireni pompano mpaka titabwerako.+ Panotu muli ndi Aroni ndi Hura.+ Aliyense amene ali ndi mlandu wofuna kuweruzidwa afikire iwowa.”+ 15 Motero Mose anakwera m’phirimo, mtambo utakuta phirilo.+

16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakutabe phirilo kwa masiku 6. Ndiyeno pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo.+ 17 Kwa ana a Isiraeli, ulemerero wa Yehova unali kuoneka ngati moto wolilima+ pamwamba pa phiri. 18 Kenako Mose analowa mumtambomo ndi kukwera m’phirimo.+ Mose anakhala mmenemo masiku 40, usana ndi usiku.+

25 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+ 2 “Uza ana a Isiraeli kuti apereke zopereka kwa ine. Anthu inu mulandire zopereka zanga kwa munthu aliyense amene mtima wake wamulimbikitsa.+ 3 Zopereka zimene muyenera kulandira kwa iwo ndi izi: golide,+ siliva,+ mkuwa,+ 4 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ubweya wa mbuzi.+ 5 Mulandirenso kwa iwo zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,+ 6 mafuta a nyale,+ mafuta a basamu+ opangira mafuta odzozera,+ ndi zofukiza zonunkhira.+ 7 Komanso mulandire miyala ya onekisi ndi miyala yozika pa efodi*+ ndi pachovala pachifuwa.+ 8 Ndipo mundipangire malo opatulika, popeza ndiyenera kukhala pakati panu.+ 9 Mukapange chihema chopatulika ndi ziwiya zake mogwirizana ndendende ndi zonse zimene ndikukusonyeza.+

10 “Mundipangire Likasa la mtengo wa mthethe,+ mikono* iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake. 11 Kenako ulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe ulikute ndi golide, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+ 12 Ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo.+ 13 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide.+ 14 Ulowetse mitengo yonyamulirayo mumphete zija za m’mbali mwa Likasa kuti azinyamulira Likasalo. 15 Mitengo yonyamulirayo izikhala mumphete za Likasalo. Isachotsedwemo.+ 16 M’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa.+

17 “Kenako upange chivundikiro chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+ 18 Upangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo uwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 19 Uike kerubi mmodzi kumbali imodzi ya chivundikirocho ndi kerubi wina kumbali inayo.+ Akerubiwo uwaike kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho. 20 Ndipo akweze mapiko awo m’mwamba ali otambasula, aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo akhale moyang’anizana,+ koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro. 21 Chivundikirocho+ uchiike pamwamba pa Likasalo, ndipo m’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa. 22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikiro,+ pakati pa akerubi awiriwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni. Kuchokera pamenepo ndidzakulamula zonse zokhudza ana a Isiraeli.+

23 “Ndiyeno upange tebulo+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake. 24 Ulikute ndi golide woyenga bwino, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+ 25 Ulipangirenso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli lizungulire tebulo lonse ndipo upange mkombero wagolide pafelemulo.+ 26 Tebulolo ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi mmene muli miyendo yake inayi.+ 27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+ 28 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi azinyamulira tebulolo.+

29 “Ndiyeno upange mbale zake, zikho, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Uzipange ndi golide woyenga bwino.+ 30 Ndipo patebulopo uziikapo mkate wachionetsero pamaso panga nthawi zonse.+

31 “Kenako upange choikapo nyale chagolide woyenga bwino. Chimenechi chikhale chosula.+ Choikapo nyalecho chikhale ndi tsinde, nthambi, masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa. 32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6, kumbali ina kutuluke nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kutulukenso nthambi zitatu.+ 33 Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, pakhalenso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+ Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zikhale zotero. 34 Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+ 35 Mfundo imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+ 36 Choikapo nyalecho chikhale ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chisulidwe monga chiwiya chimodzi, chagolide woyenga bwino.+ 37 Ndipo uchipangire nyale 7. Nyalezo ziziyatsidwa kuti ziziunikira patsogolo pake.+ 38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+ 39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.* 40 Uonetsetse kuti wazipanga motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.+

26 “Ndiyeno upange chihema chopatulika ndi nsalu 10 zopangira hema.+ Nsaluzo zikhale zaulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ ndi ulusi wofiira kwambiri. Pansaluzo upetepo akerubi.+ 2 M’litali mwake, nsalu iliyonse ikhale mikono 28, ndipo m’lifupi mwake ikhale mikono inayi. Nsalu zonse muyezo wake ukhale wofanana.+ 3 Nsalu zisanu zikhale zolumikizana, ndipo zina zisanu zikhalenso zolumikizana.+ 4 Ndipo uike zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu imodzi mwa nsalu zolumikizanazo. Uchitenso chimodzimodzi kumapeto kwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi.+ 5 Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu imene ili polumikizirana nsalu ziwirizo. Zingwezo zikhale moyang’anizana.+ 6 Upangenso ngowe 50 zagolide ndi kulumikiza nsalu za chihema chopatulika zija ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+

7 “Upange nsalu za ubweya wa mbuzi+ zoyala pachihema chopatulika. Upange nsalu 11. 8 M’litali nsalu iliyonse ikhale mikono 30,+ ndipo m’lifupi nsalu iliyonse ikhale mikono inayi. Nsalu zonse 11 zija muyezo wake ukhale wofanana. 9 Ulumikize nsalu zisanu pazokha, kenako ulumikizenso nsalu 6 pazokha,+ ndipo upinde pakati nsalu ya 6 ya koyambirira kwa nsalu zolumikizanazo. 10 Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu yakumapeto kwenikweni kwa nsalu za chihema zolumikizanazo. Uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu zina zolumikizana, pomwe magulu awiri a nsalu zolumikizanalumikizanazo adzakumane. 11 Ndiyeno upange ngowe 50 zamkuwa+ ndi kuzilowetsa m’zingwe zopota zokolekamo ngowezo, n’kulumikiza nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+ 12 Ndipo nsalu yotsala ya chinsalucho itsike mpaka m’munsi. Hafu yake yotsala ilendewere mpaka m’munsi, kumbuyo kwa chihema chopatulika. 13 Ndipo m’litali mwa chinsalu chija, mkono umodzi kumbali iyi ndi mkono umodzinso kumbali inayo, zikhale zolendewera mpaka m’munsi m’mbali mwa chihema chopatulika, kuphimba chihemacho mbali iyi ndi mbali inayo.

14 “Ndiyeno upange chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu.

15 “Upange mafelemu oimika+ a chihema chopatulika a matabwa a mthethe. 16 M’litali mwake, felemu lililonse likhale mikono 10, ndipo m’lifupi mwake felemu lililonse likhale mkono umodzi ndi hafu. 17 Felemu lililonse likhale ndi mano awiri oyandikana. Mafelemu onse a chihema chopatulika uwapange motero. 18 Upange mafelemu 20 a chihema chopatulika omangira mbali ya kum’mwera ya chihemacho, yoyang’ana ku Negebu.

19 “Upange zitsulo 40 zasiliva zamphako+ zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri. 20 Kumbali inayo ya chihema chopatulika, chakumpoto, kukhale mafelemu 20,+ 21 ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri.+ 22 Ndipo kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo, upangireko mafelemu 6.+ 23 Ndiyeno upange mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza m’makona akumbuyo a chihema chopatulika.+ 24 Lililonse la mafelemu amenewa likhale ndi matabwa awiri ofanana kuyambira pansi mpaka pamwamba. Matabwawo alumikizane pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo apangidwe mofanana ndipo akhale ochirikiza m’makona. 25 Pakhale mafelemu 8 ndi zitsulo zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo 16 zokhazikapo mafelemu, ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri.

26 “Upangenso mipiringidzo ya mtengo wa mthethe,+ mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali imodzi ya chihema chopatulika. 27 Mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali ina ya chihema chopatulika, mipiringidzo inanso isanu yogwira mafelemu akumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo.+ 28 Mpiringidzo wapakati ugwire mafelemu onse kuyambira kumapeto mpaka kumapeto.

29 “Ukute mafelemuwo ndi golide,+ ndipo mphete zake, zolowetsamo mipiringidzo, uzipange ndi golide. Mipiringidzoyo uikute ndi golide. 30 Umange chihema chopatulikacho motsatira pulani imene ndakuonetsa m’phiri.+

31 “Upange nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi upetepo akerubi.+ 32 Nsalu imeneyi uipachike pamizati inayi ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyi tikhale tagolide. Mizati imeneyi ikhale pazitsulo zinayi zasiliva zamphako. 33 Nsalu yotchingayi uipachike m’munsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la umboni+ kuseri kwa nsalu yotchingayi. Nsaluyi ikhale malire pakati pa Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+ 34 Ukatero uike chivundikiro pamwamba pa likasa la umboni m’Malo Oyera Koposa.

35 “Kenako uike tebulo kunja kwa nsalu yotchinga ndipo uikekonso choikapo nyale.+ Chimenechi chikhale moyang’anizana ndi tebulo kumbali ina ya chihema chopatulika, chakum’mwera. Tebulo uliike chakumpoto. 36 Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga+ khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ya ulusi wofiira kwambiri, ndi ya ulusi wopota wabwino kwambiri. 37 Nsalu yotchinga khomo la chihema uipangire mizati isanu ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyo tikhale tagolide. Ndipo upange zitsulo zamkuwa zisanu zamphako zokhazikapo mizatiyo.

27 “Upange guwa lansembe la matabwa a mthethe, m’litali mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo+ likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake likhale mikono itatu. 2 Upange nyanga m’makona ake anayi. Nyanga+ zakezo zituluke m’makona akewo, ndipo ulikute ndi mkuwa.+ 3 Kenako upange ndowa zake zochotsera phulusa losakanizika ndi mafuta, mafosholo ake, mbale zake zolowa, mafoloko aakulu, ndi zopalira moto zake. Ziwiya zake zonse uzipange ndi mkuwa.+ 4 Upangenso sefa wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana,+ ndipo pasefayo upange mphete zinayi zamkuwa m’makona ake anayi. 5 Ulowetse sefayo chapakati pa guwa lansembe, m’munsi mwa mkombero.+ 6 Guwalo ulipangire mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe, ndipo uikute ndi mkuwa.+ 7 Mitengo yonyamulirayo uziilowetsa mumphetezo kumbali ziwiri za guwalo polinyamula.+ 8 Upange bokosi lamatabwa losatseka pansi. Alipange mmene iye wakusonyezera m’phiri.+

9 “Ndiyeno upange bwalo+ la chihema chopatulika. Kumbali ya ku Negebu, chakum’mwera, bwalolo ulitchinge ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Mpandawo ukhale mikono 100 m’litali mwake kumbali imodziyo. 10 Upangenso nsanamira zake 20 ndi zitsulo zamkuwa 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi mfundo zake zikhale zasiliva.+ 11 Mpandawo kumbali yakumpoto, m’litali mwake ukhalenso momwemo. Nsalu yampandawo ikhale mikono 100 m’litali mwake, ndipo kukhale nsanamira 20 ndi zitsulo zamkuwa 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi mfundo zake zikhale zasiliva.+ 12 M’lifupi mwa bwalolo, kumbali ya kumadzulo, mpanda wa nsaluwo ukhale mikono 50 kutalika kwake, ndipo kukhale nsanamira 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo nsanamirazo.+ 13 Ndipo m’lifupi mwa bwalolo kumbali ya kum’mawa, kotulukira dzuwa, kukhale mikono 50.+ 14 Kudzanja lamanja la chipata cha bwalolo, mpanda wa nsaluwo ukhale mikono 15 kutalika kwake. Kukhale nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+ 15 Ndipo kudzanja lamanzere la chipata cha bwalolo kukhale nsalu za mpanda mikono 15. Kukhale nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+

16 “Pachipata cha bwalo pakhale nsalu yowomba m’litali mwake ikhale mikono 20, ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+ Pakhale nsanamira zinayi ndi zitsulo zinayi zokhazikapo nsanamirazo.+ 17 Nsanamira zonse kuzungulira bwalo lonselo zikhale ndi mfundo zasiliva, ndipo tizitsulo tokolowekapo nsalu tikhale tasiliva, koma zitsulo zokhazikapo nsanamirazo zikhale zamkuwa.+ 18 Bwaloli m’litali mwake likhale mikono 100,+ m’lifupi mwake mikono 50, ndipo msinkhu wake mikono isanu. Nsalu zake zikhale za ulusi wopota, wabwino kwambiri, ndipo zitsulo zake zokhazikapo nsanamira zikhale zamkuwa. 19 Ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wonse wa pachihema chopatulika, zikhomo zonse za chihema, ndi zikhomo za bwalo zikhale zamkuwa.+

20 “Koma iwe, ulamule ana a Isiraeli kuti akupezere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 21 M’chihema chokumanako,* kunja kwa nsalu yotchinga+ pafupi ndi Umboni, Aroni ndi ana ake azikhazika nyale pamalo ake, kuunikira pamaso pa Yehova,+ kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa ana a Isiraeli+ kuti mibadwo yawo izichita zimenezi mpaka kalekale.+

28 “Koma iwe patula Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli, ndipo Aroniyo+ atumikire monga wansembe wanga pamodzi ndi ana akewo,+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+ 2 Aroni m’bale wako umupangire zovala zopatulika kuti zimupatse ulemerero ndi kum’kongoletsa.+ 3 Ndipo iwe ulankhule ndi anthu onse aluso amene ndinadzaza mzimu wa nzeru+ m’mitima yawo kuti amupangire Aroni zovala zomuyeretsa, kuti atumikire monga wansembe wanga.+

4 “Zovala zoti apange ndi izi: chovala pachifuwa,+ efodi,*+ malaya akunja odula manja,+ mkanjo wamandalasi, nduwira+ ndi lamba wa pamimba.+ Apange zovala zopatulika za Aroni m’bale wako ndi ana ake, kuti atumikire monga wansembe wanga. 5 Ndipo iwo atenge golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.

6 “Ndipo apange efodi wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+ 7 Pakhale nsalu ziwiri za m’mapewa ndipo azilumikize pa efodiyo, azilumikize pamapewa.+ 8 Ndipo lamba womangira efodi,+ wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.

9 “Utenge miyala iwiri ya onekisi+ ndi kulembapo+ mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba.+ 10 Mayina 6 uwalembe pamwala umodzi ndipo mayina 6 otsalawo uwalembe pamwala winawo motsatira mmene anabadwira.+ 11 Ugwiritse ntchito mmisiri wogoba kuti alembe mayina a ana a Isiraeli pamiyala iwiriyo mwaluso la wogoba miyala.+ Awalembe ngati mmene amagobera chidindo. Apange miyalayo moti izitha kulowa m’zoikamo zake zagolide.+ 12 Ndipo ulowetse miyala iwiriyo pansalu za m’mapewa za efodi kuti ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Isiraeli.+ Poonekera kwa Yehova, Aroni azidzanyamula mayina awo pansalu ziwiri za m’mapewa ake kuti chikhale chikumbutso. 13 Upange zoikamo miyala zagolide, 14 ndi matcheni awiri agolide woyenga bwino.+ Uwapange ngati zingwe zopota mwaluso, ndipo ulumikize matcheni okhala ngati zingwewo ku zoikamo miyala.+

15 “Upange chovala pachifuwa chachiweruzo+ chopeta mwaluso. Uchipange mwaluso mofanana ndi efodi. Uchipange ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+ 16 Ukachipinda pakati chizikhala chofanana mbali zonse zinayi, m’litali mwake chizikhala chikhatho* chimodzi ndipo m’lifupi mwake chikhatho chimodzi.+ 17 Uikepo miyala ndipo ikhale m’mizere inayi.+ Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rube,+ topazi+ ndi emarodi.+ 18 Mzere wachiwiri ukhale ndi miyala ya nofeki,+ safiro+ ndi yasipi.+ 19 Mzere wachitatu ukhale ndi miyala ya lesemu, sibu+ ndi ametusito.+ 20 Mzere wa chinayi ukhale ndi miyala ya kulusolito,+ onekisi+ ndi yade. Zoikamo miyala zake zikhale zagolide.+ 21 Miyalayo uiike malinga ndi mayina a mafuko a ana a Isiraeli, malinga ndi mayina a mafuko awo 12.+ Miyalayo ikhale yolembedwa mogoba ngati mmene amagobera chidindo, mwala uliwonse ukhale ndi limodzi mwa mayina a mafuko 12.+

22 “Pachovala pachifuwa upangepo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+ 23 Upange mphete ziwiri zagolide pachovala pachifuwa,+ mphete ziwirizo uziike m’makona awiri a chovala pachifuwacho. 24 Ndiyeno upise zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zomwe zili m’makona a chovala pachifuwa.+ 25 Ndipo ulowetse zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri zimene zili pansalu za m’mapewa za efodi chapatsogolo pake.+ 26 Upange mphete ziwiri zagolide ndi kuziika m’makona awiri a chovala pachifukwa kumbali yopindira mkati yokhudzana ndi efodi.+ 27 Upangenso mphete ziwiri zagolide ndi kuziika pansalu ziwiri za pamapewa za efodi m’munsi mwake, kutsogolo kwa nsaluzo, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba wa efodi.+ 28 Ndipo azimanga chovala pachifuwa ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chilowe mumphete za chovala pachifuwa ndi mphete za efodi, kuti chovala pachifuwacho chizikhala pamwamba pa lamba wa efodi, kutinso chisasunthe pa efodipo.+

29 “Ndipo Aroni azinyamula mayina a ana a Isiraeli pamtima pake, pachovala pachifuwa chachiweruzo, pamene akulowa m’Malo Oyera kuti chikhale chikumbutso pamaso pa Yehova nthawi zonse. 30 Ndiyeno uike Urimu+ ndi Tumimu m’chovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamalowa kukaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula ziweruzo+ za ana a Isiraeli pamtima pake poonekera kwa Yehova nthawi zonse.

31 “Ndiyeno upange malaya odula manja ndi ulusi wabuluu wokhawokha, ovala mkati mwa efodi.+ 32 Malayawo akhale otsegula pamwamba pake, pakatikati. Potsegulapo pakhale popenderera m’mphepete mwake ndi nsalu yowomba. Pakhale potsegula ngati chovala cha kunkhondo chamamba achitsulo, kuti pasang’ambike.+ 33 Mumpendero wake wa m’munsi upangemo makangaza* a ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri kuzungulira mpenderowo. Upangenso mabelu+ agolide pakati pa makangazawo kuzungulira mpenderowo. 34 Pakhale belu lagolide ndi khangaza, belu lagolide ndi khangaza kuzungulira mpendero wa m’munsi mwa malaya odula manjawo.+ 35 Aroni azivala zimenezo kuti atumikire, ndipo mabeluwo azimveka iye akamalowa m’malo opatulika pamaso pa Yehova ndi pamene akutuluka, kuti asafe.+

36 “Upangenso kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti, ‘Chiyero n’cha Yehova.’+ 37 Kachitsulo kameneko ukamangirire panduwira+ ndi chingwe chabuluu. Kazikhala patsogolo pa nduwirayo. 38 Chotero kachitsuloko kazikhala pamphumi pa Aroni, ndipo Aroni aziyankha mlandu wa machimo ochimwira zinthu zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli adzaziyeretsa. Izi ndizo mphatso zawo zonse zopatulika. Kachitsuloko kazikhala pamphumi pake nthawi zonse, kuti azichititsa anthuwo kukhala ovomerezeka+ pamaso pa Yehova.

39 “Kenako uwombe mkanjo wamandalasi ndi ulusi wabwino kwambiri. Upangenso nduwira ya nsalu yabwino kwambiri,+ ndiponso uwombe lamba+ wa mkanjo.

40 “Ana a Aroni uwapangire mikanjo+ ndi malamba ake. Uwapangirenso mipango*+ yokulunga kumutu kuti iwapatse ulemerero ndi kuwakongoletsa.+ 41 Ndipo uveke Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake zinthu zimenezi. Ukatero uwadzoze,+ uwapatse mphamvu*+ ndi kuwayeretsa, ndipo atumikire monga ansembe anga. 42 Ndipo uwapangire makabudula ansalu ofika m’ntchafu kuti azibisa maliseche awo.+ 43 Aroni ndi ana ake azivala makabudula amenewa polowa m’chihema chokumanako kapena popita kuguwa lansembe kukatumikira pamalo oyera, kuti asapalamule mlandu ndi kufa. Limeneli ndi lamulo kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale.+

29 “Tsopano uchite izi kwa iwo kuti uwayeretse atumikire monga ansembe anga: Utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo,+ zopanda chilema,+ 2 mkate wopanda chofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati, wopanda chofufumitsa, wothira mafuta ndi timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala. 3 Zimenezi uziike m’dengu ndi kuzipereka zili m’dengu momwemo.+ Uchitenso chimodzimodzi ndi ng’ombe ndi nkhosa ziwiri zija.

4 “Ndiyeno ubweretse Aroni ndi ana ake pakhomo+ la chihema chokumanako, ndipo uwalamule kuti asambe ndi madzi.+ 5 Kenako utenge zovala+ zija ndi kuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi.* Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa. Efodiyo um’mange bwino ndi lamba wake.+ 6 Ndiyeno umuveke nduwira pamutu pake ndipo panduwirapo uikepo chizindikiro chopatulika cha kudzipereka.+ 7 Kenako utenge mafuta odzozera+ ndi kuwathira pamutu pake ndi kum’dzoza.+

8 “Ukatero utenge ana ake ndi kuwaveka mikanjo.+ 9 Ndiyeno Aroni ndi ana akewo uwamange malamba a pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo unsembe udzakhala wawo. Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale.+ Choncho upatse Aroni ndi ana ake mphamvu. +

10 “Kenako upereke ng’ombe patsogolo pa chihema chokumanako, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa ng’ombeyo.+ 11 Ndiyeno ng’ombeyo uiphe pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ 12 Ukatero utengeko magazi a ng’ombeyo+ ndi chala chako ndi kuwapaka panyanga za guwa lansembe.+ Otsalawo uwathire pansi, paguwa lansembe.+ 13 Utenge mafuta+ onse okuta matumbo,+ mafuta a pachiwindi,*+ impso ziwiri ndi mafuta ake, n’kuzitentha* paguwa lansembe.+ 14 Koma nyama ya ng’ombeyo, chikopa chake ndi ndowe zake uzitenthe ndi moto kunja kwa msasa.+ Ng’ombeyo ndi nsembe yamachimo.

15 “Ndiyeno utenge nkhosa imodzi,+ ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 16 Nkhosayo uiphe ndi kutenga magazi ake ndi kuwawaza mozungulira paguwa lansembelo.+ 17 Pamenepo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake ndi kuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18 Nkhosa yonseyo uitenthe paguwa lansembe. Imeneyo ndi nsembe yopsereza+ yoperekedwa kwa Yehova, fungo lokhazika mtima pansi.+ Ndiyo nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

19 “Kenako utenge nkhosa inayo, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 20 Akatero, uphe nkhosayo ndi kutengako magazi ake ndi kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la Aroni, ndi m’munsi pamakutu a kudzanja lamanja a ana a Aroni. Uwapakenso pazala zawo za manthu kudzanja lamanja ndi pazala zawo zazikulu za kumwendo wa kumanja,+ ndipo uwaze magaziwo mozungulira paguwa lansembe. 21 Ndiyeno utengeko magazi amene ali paguwa lansembe ndi mafuta pang’ono odzozera,+ ndi kuwadontheza pa Aroni ndi pazovala zake. Uwadonthezenso pa ana ake ndi zovala zawo kuti Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake ndi zovala zawo akhale oyera.+

22 “Ndiyeno kunkhosayo utengeko mafuta ndi mchira wa mafuta+ ndi mafuta okuta matumbo, mafuta a pachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja,+ pakuti nkhosayo ndi yowalongera unsembe.+ 23 M’dengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mtanda wobulungira wa mkate, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala.+ 24 Zonsezi uziike m’manja mwa Aroni ndi m’manja mwa ana ake,+ ndi kuziweyulira* uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ 25 Ndiyeno uzitenge m’manja mwawo ndi kuzitentha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza, kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ Ndiyo nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+

26 “Kenako utenge nganga ya nkhosa yolongera Aroni unsembe,+ ndi kuiweyulira uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyo ikhale gawo lako. 27 Pa nkhosa yolongera Aroni ndi ana ake unsembe,+ upatule nganga+ ya nsembe yoweyula imene anaweyula, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka. 28 Zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake mwa lamulo mpaka kalekale. Ana a Isiraeli ayenera kutsatira lamulo limeneli chifukwa ndi gawo lopatulika.+ Lidzakhala gawo lopatulika loyenera kuperekedwa ndi ana a Isiraeli. Limeneli ndi gawo lawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova kuchokera pansembe zawo zachiyanjano.+

29 “Zovala zopatulika+ za Aroni zidzakhala za ana ake+ obwera m’mbuyo mwake. Adzawadzoza+ ndi kuwapatsa mphamvu atavala zovala zimenezi.+ 30 Wansembe amene adzalowa m’malo mwake kuchokera pakati pa ana ake, amene adzalowa m’chihema chokumanako kukatumikira m’malo oyera azidzavala zovalazo kwa masiku 7.+

31 “Kenako utenge nkhosa yowalongera unsembe ndi kuwiritsa nyama yake m’malo oyera.+ 32 Ndipo Aroni ndi ana ake adye+ nyama ya nkhosayo ndi mkate umene uli m’dengu, adyere pakhomo la chihema chokumanako. 33 Adye zinthu zimene aphimbira machimo kuti apatsidwe mphamvu ndi kuyeretsedwa.+ Koma munthu wamba asadye nawo, chifukwa ndi zinthu zopatulika.+ 34 Nyama ya nkhosa yowalongera unsembe ndi mkatewo, zikatsala mpaka m’mawa mwake, uzitenthe ndi moto.+ Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zinthu zopatulika.

35 “Uchite zimenezi kwa Aroni ndi ana ake malinga ndi zonse zimene ndakulamula.+ Udzatenga masiku 7 kuti uwapatse mphamvu. + 36 Choncho uzipereka ng’ombe ya nsembe yamachimo tsiku ndi tsiku kuti iphimbe machimo.+ Pamenepo uziyeretsa guwa lansembe ku machimo mwa kuliperekera nsembe yophimba machimo, ndipo uzilidzoza+ kuti likhale loyera. 37 Udzatenga masiku 7 poperekera guwa lansembelo nsembe yophimba machimo. Udzaliyeretse+ kuti likhale guwa lansembe loyera koposa.+ Aliyense wokhudza guwa lansembe azikhala woyera.+

38 “Zimene uzipereka paguwa lansembelo ndi izi: ana a nkhosa a chaka chimodzi, awiri pa tsiku nthawi zonse.+ 39 Uzipereka mwana wa nkhosa mmodzi m’mawa,+ ndipo mwana wa nkhosa winayo madzulo kuli kachisisira.*+ 40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala,+ muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo anayi a vinyo wa nsembe yachakumwa.+ 41 Ndiyeno uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira. Um’pereke pamodzi ndi nsembe yambewu+ yofanana ndi ya m’mawa komanso ndi nsembe yake yachakumwa. Uzipereke monga fungo lokhazika mtima pansi, nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. 42 M’mibadwo yanu yonse, muzipereka nsembe yopsereza imeneyi nthawi zonse+ pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova, kumene ndidzaonekera kwa inu kuti ndilankhule nanu.+

43 “Chotero ndidzaonekera pamenepo kwa ana a Isiraeli, ndipo malo amenewa adzayeretsedwa ndi ulemerero wanga.+ 44 Ndidzayeretsa chihema chokumanako ndi guwa lansembe. Ndidzayeretsanso+ Aroni ndi ana ake kuti atumikire monga ansembe anga. 45 Choncho ndidzakhala pakati pa ana a Isiraeli, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo.+ 46 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo kuti ndikhale pakati pawo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wawo.+

30 “Upange guwa lansembe la zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa a mthethe. 2 M’litali mwake likhale mkono umodzi, m’lifupi mwake mkono umodzi. Mbali zake zonse zinayi zikhale zofanana, ndipo msinkhu wake ukhale mikono iwiri. Guwalo likhale ndi nyanga pamwamba pake.+ 3 Ndiyeno ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake, ndi m’mbali mwake kuzungulira guwalo, komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.+ 4 Kumbali ziwiri za guwalo upangeko mphete zagolide, ziwiri kumbali iyi ndi zinanso ziwiri kumbali inayo. Uzipange m’munsi mwa mkombero kuti muzilowa mitengo yonyamulira guwalo.+ 5 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo uikute ndi golide.+ 6 Guwalo uliike kutsogolo kwa nsalu yotchinga imene ili pafupi ndi likasa la umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni,* pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+

7 “Aroni azifukiza zofukiza zonunkhira paguwapo.+ M’mawa uliwonse akamasamalira nyale,+ azifukiza zofukizazo. 8 Aziteronso akamayatsa nyalezo madzulo.* Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse m’mibadwo yanu yonse. 9 Paguwali usaperekepo zofukiza zosaloleka,+ nsembe yopsereza kapena nsembe yambewu, ndipo usathirepo nsembe yachakumwa. 10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo yophimbira machimo,+ panyanga za guwalo kuti aziphimbira machimo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ m’mibadwo yanu yonse. Kwa Yehova, guwalo ndi lopatulika koposa.”

11 Pamenepo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 12 “Ukamachita kalembera pa ana a Isiraeli, + aliyense wa iwo azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi yowawerengayo,+ kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.+ 13 Owerengedwa onse ayenera kupereka zotsatirazi: hafu ya sekeli yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli limodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+ 14 Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo azipereka choperekacho kwa Yehova.+ 15 Pamene mukupereka kwa Yehova chopereka chokuphimbirani machimo,+ anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.+ 16 Choncho ulandire ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa pachihema chokumanako+ monga dipo la miyoyo yanu, pophimba machimo anu, kuti Yehova akumbukire ana a Isiraeli.”

17 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 18 “Upange beseni losambira lamkuwa ndi choikapo chake chamkuwa.+ Uliike pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe, ndipo uthiremo madzi.+ 19 Pamenepo Aroni ndi ana ake azisamba m’manja ndi mapazi awo.+ 20 Polowa m’chihema chokumanako, kapena popita kukatumikira paguwa lansembe, kukapereka kwa Yehova nsembe yotentha ndi moto,+ azisamba kuti asafe. 21 Azisamba m’manja ndi mapazi awo kuti asafe.+ Limeneli ndi lamulo kwa iwo mpaka kalekale, likhale lamulo kwa Aroni ndi ana ake ku mibadwo yawo yonse.”+

22 Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 23 “Koma iweyo utenge mafuta awa onunkhira, abwino koposa:+ madontho oundana a mule*+ masekeli 500, sinamoni*+ wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi* wonunkhira+ wokwana masekeli 250. 24 Utengenso kasiya*+ masekeli 500 olingana ndi masekeli a kumalo oyera+ ndi mafuta a maolivi hini+ imodzi. 25 Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakaniza mwaluso.+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.+

26 “Mafuta amenewa udzozere chihema chokumanako,+ likasa la umboni, 27 tebulo ndi ziwiya zake zonse, choikapo nyale ndi ziwiya zake zonse, guwa lansembe zofukiza, 28 guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, komanso beseni ndi choikapo chake. 29 Ndipo uziyeretse kuti zikhale zoyera koposa.+ Aliyense wogwira zinthu zimenezi azikhala woyera.+ 30 Udzoze Aroni+ ndi ana ake,+ ndipo uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga.+

31 “Ndiyeno uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Mafuta awa akhale mafuta anga ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika m’mibadwo yanu yonse.+ 32 Musapake mafuta amenewa pakhungu la munthu aliyense, ndipo musapange mafuta ofanana nawo pogwiritsa ntchito zinthu zopangira mafutawa. Mafuta amenewa ndi opatulika. Apitirizebe kukhala opatulika kwa inu. 33 Aliyense wopanga mafuta ofanana ndi amenewa, ndiponso amene angapake munthu wamba, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”+

34 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Tenga zonunkhira izi:+ madontho a sitakate,* onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani*+ weniweni. Zonsezi zikhale za muyezo wofanana. 35 Zinthu zimenezi upangire zofukiza,+ msanganizo wa zonunkhiritsa zosakaniza mwaluso, wothira mchere,+ msanganizo weniweni wopatulika. 36 Kenako upere wina mwa msanganizo umenewu kuti ukhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni m’chihema chokumanako,+ kumene ndidzaonekera kwa iwe.+ Msanganizowu ukhale wopatulika koposa kwa inu. 37 Musapange zofukiza zanuzanu pogwiritsa ntchito zinthu zopangira msanganizo umenewu.+ Inu muziona zofukiza zimenezi kukhala zopatulika kwa Yehova.+ 38 Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kudzisangalatsa ndi kununkhira kwake, adzaphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.”

31 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Inetu ndikuitana ndi kutchula dzina Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndipo ndidzam’patsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse.+ 4 Ndidzam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,+ 5 waluso lolemba pamiyala mochita kugoba+ ndi wodziwa kupanga zinthu zina zilizonse zamatabwa.+ 6 Ndipo inetu ndaika Oholiabu mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani+ kuti athandize Bezaleli. Komanso ndaika nzeru mumtima wa munthu aliyense waluso, kuti apange zonse zimene ndakulamulazi:+ 7 chihema chokumanako,+ likasa+ la umboni, chivundikiro chimene chili pamwamba pake,+ ndi zipangizo zonse za m’chihema. 8 Kutinso apange tebulo ndi zipangizo zake,+ choikapo nyale chagolide woyenga bwino ndi zipangizo zake zonse,+ guwa lansembe zofukiza,+ 9 guwa lansembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse,+ beseni ndi choikapo chake,+ 10 zovala zosokedwa bwino ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe,+ 11 mafuta odzozera, ndi zofukiza zonunkhira za pamalo opatulika.+ Iwo adzapanga zonse malinga ndi zimene ndakulamula.”

12 Kenako Yehova anauzanso Mose kuti: 13 “Koma iwe uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti muzisunga masiku anga a sabata,+ pakuti ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu m’mibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.+ 14 Muzisunga sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Amene walinyoza ayenera kuphedwa ndithu.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la sabata adzaphedwa ndithu. 16 Ana a Isiraeli azisunga sabata, ndipo azichita zimenezi m’mibadwo yawo yonse. Limeneli ndi pangano mpaka kalekale.+ 17 Chimenechi n’chizindikiro pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa m’masiku 6, Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo pa tsiku la 7 anapuma pa ntchito yake.’”+

18 Ndiyeno atamaliza kulankhula naye paphiri la Sinai, anapatsa Mose miyala iwiri yosema ya Umboni,+ miyala yolembedwapo mawu ndi chala cha Mulungu.+

32 Mose ali m’phirimo, anthu anaona kuti akuchedwa kutsika.+ Chotero anthuwo anasonkhana kwa Aroni ndi kumuuza kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”+ 2 Pamenepo Aroni anawauza kuti: “Vulani ndolo* zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.” 3 Choncho anthu onse anayamba kuvula ndolo zagolide zimene anavala ndi kuzipereka kwa Aroni. 4 Pamenepo iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anam’panga+ kukhala fano la mwana wa ng’ombe+ lopangidwa ndi golide wosungunula. Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+

5 Aroni ataona zimenezi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa fanolo. Kenako iye anafuula kuti: “Mawa kuli chikondwerero cha Yehova.” 6 Choncho pa tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka m’mamawa, ndi kuyamba kupereka nsembe zopsereza ndi zachiyanjano. Atatero, iwo anakhala pansi ndi kudya ndiponso kumwa. Kenako anaimirira n’kuyamba kusangalala.+

7 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Pita, tsika, chifukwa anthu ako amene unawatsogolera potuluka m’dziko la Iguputo achita zinthu zowawonongetsa.+ 8 Apatuka mofulumira panjira imene ndawalamula kuyendamo.+ Iwo adzipangira fano la mwana wa ng’ombe lopangidwa ndi golide wosungunula. Akuligwadira ndi kupereka nsembe kwa fanolo, ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka m’dziko la Iguputo.’”+ 9 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ndawayang’ana anthu amenewa, ndipo ndaona kuti ndi anthu ouma khosi.+ 10 Ndileke tsopano kuti mkwiyo wanga uwayakire ndipo ndiwafafanize,+ koma iwe ndikupange kukhala mtundu waukulu.”+

11 Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.+ Iye anati: “N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu+ uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu? 12 Aiguputo+ anenerenji kuti, ‘Anawatulutsa m’dziko lino kuti akawaphe kumapiri ndi kuwafafaniza padziko lapansi’?+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo,+ ndipo mverani chisoni+ anthu anu kuti musawagwetsere tsoka. 13 Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira pa inu mwini,+ powauza kuti, ‘Ndidzachulukitsa mbewu yanu ngati nyenyezi zakumwamba,+ ndipo dziko lonseli limene ndalipatula ndidzalipereka kwa mbewu yanu,+ kuti likhale lawo mpaka kalekale.’”+

14 Pamenepo, Yehova anayamba kumva chisoni chifukwa cha tsoka limene ananena kuti agwetsera anthu ake.+

15 Kenako, Mose anatembenuka n’kutsika m’phirimo+ atanyamula miyala yosema ya Umboni+ m’manja mwake. Miyalayo inali yolembedwapo mawu mbali zonse ziwiri. Inali yolembedwapo mawu mbali iyi ndi mbali inayo. 16 Miyalayo inapangidwa ndi Mulungu, ndipo mawuwo analembedwapo ndi Mulungu mochita kugoba.+ 17 Ndiyeno Yoswa anayamba kumva phokoso la kufuula kwa anthu, chotero anauza Mose kuti: “Kukumveka phokoso lankhondo+ kumsasa.” 18 Koma Mose anati:

“Limeneli si phokoso la nyimbo ya kupambana,+

Komanso si nyimbo yachisoni chifukwa chogonjetsedwa;

Ndikumva ngati ndi kuimba kwa mtundu wina.”

19 Chotero atayandikira msasawo n’kuona mwana wa ng’ombe+ ndi anthu akuvina, mkwiyo wa Mose unayaka ndipo nthawi yomweyo anaponya pansi miyala ija ndi kuiswa ali m’tsinde mwa phiri.+ 20 Ndiyeno anatenga mwana wa ng’ombe amene iwo anapanga n’kumutentha ndi moto ndi kum’pera mpaka atakhala fumbi.+ Kenako anamwaza fumbilo pamadzi+ ndi kuwamwetsa Aisiraeli.+ 21 Atatero, Mose anafunsa Aroni kuti: “Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti udzetse tchimo lalikulu chonchi pa iwo?” 22 Ndipo Aroni anayankha kuti: “Mkwiyo wa mbuyanga usayake. Inuyo mukuwadziwa bwino anthuwa, kuti amakonda kuchita zoipa.+ 23 Iwo anandiuza kuti, ‘Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.’ 24 Choncho ndinawauza kuti, ‘Ndani wavala zagolide? Avule zimenezo ndi kundipatsa.’ Ndiyeno golideyo ndinamuponya pamoto n’kusanduka mwana wa ng’ombe ameneyu.”

25 Mose anaona kuti anthuwo akuchita zinthu motayirira, chifukwa Aroni anawalola kuchita zotayirira+ zomwe zinachititsa adani awo kuwatonza.+ 26 Ndiyeno Mose anakaima pachipata cha msasawo, ndipo anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine!”+ Ndipo ana onse aamuna a Levi anayamba kusonkhana kwa Mose. 27 Pamenepo iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake m’chiuno mwake. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa ndi kuyenda mobwerezabwereza, kuchoka pachipata china kufika pachipata china, ndipo aliyense wa inu aphe m’bale wake, mnzake ndi mnzake wapamtima.’”+ 28 Pamenepo ana a Levi+ anachita zimene Mose anawauza, moti patsiku limenelo anthu pafupifupi 3,000 anaphedwa. 29 Zitatero Mose anati: “Dzilimbitseni* lero kuti muchite utumiki kwa Yehova,+ chifukwa aliyense wa inu waukira mwana wake ndi m’bale wake,+ kuti Mulungu akupatseni dalitso lero.”+

30 Pa tsiku lotsatira, Mose anati kwa anthuwo: “Inuyo mwachita tchimo lalikulu.+ Choncho ndikwera kupita kwa Yehova kuti mwina ndikakam’chonderera angakukhululukireni tchimo lanu.”+ 31 Choncho Mose anabwerera kwa Yehova ndi kunena kuti: “Aa, anthuwa achita tchimo lalikulu, chifukwa adzipangira mulungu wagolide!+ 32 Komano ngati mukufuna kuwakhululukira tchimo lawo,+ . . . koma ngati simukufuna, ndifafanizeni+ chonde, m’buku lanu+ limene mwalemba.” 33 Komabe Yehova anauza Mose kuti: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.+ 34 Tsopano atsogolere anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu,+ ndipo pa tsiku langa lopereka chilango, ndidzawalangadi chifukwa cha tchimo lawo.”+ 35 Ndipo Yehova anagwetsera mliri pa anthuwo chifukwa cha mwana wa ng’ombe amene iwo anam’panga kudzera mwa Aroni.+

33 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Nyamukani, muchoke pano, iweyo ndi anthu amene unawatsogolera potuluka m’dziko la Iguputo.+ Mupite kudziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili kwa mbewu yako.’+ 2 Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu+ kuti akathamangitse Akanani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 3 Mupite kudziko loyenda mkaka ndi uchi,+ pakuti sindidzayenda pakati panu, pakuti ndingakufafanizeni panjira,+ chifukwa ndinu anthu ouma khosi.”+

4 Anthu atamva mawu odetsa nkhawa amenewa, anayamba kulira,+ ndipo palibe aliyense wa iwo anavala zodzikongoletsera. 5 Ndiyeno Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Inu ndinu anthu ouma khosi.+ Ndingathe kulowa pakati panu ndi kukufafanizani m’kamphindi.+ Chotero, vulani zodzikongoletsera, pakuti ndikufuna kuona choti ndikuchiteni.’”+ 6 Pamenepo ana a Isiraeli anavula zodzikongoletsera ali kuphiri la Horebe+ ndipo sanazivalenso.

7 Zitatero, Mose anatenga hema wake ndi kukam’manga kunja kwa msasa, kutali kwambiri ndi msasawo, ndipo anatcha hemayo dzina lakuti chihema chokumanako. Aliyense wofuna kufunsira+ kwa Yehova anali kupita kuchihema chokumanako, chimene chinali kunja kwa msasa. 8 Ndiyeno Mose akatuluka mumsasawo kupita kuchihema, anthu onse anali kuimirira.+ Aliyense anali kuimirira pakhomo la hema wake, n’kumayang’anitsitsa Mose kufikira atalowa m’chihema. 9 Ndipo Mose akangolowa m’chihema, mtambo woima njo ngati chipilala+ unali kutsika ndi kuima pakhomo la chihemacho. Zikatero Mulungu anali kulankhula+ ndi Mose. 10 Anthu onse anali kuona mtambowo+ utaima pakhomo la chihema, ndipo onse anali kuimirira ndi kugwada, aliyense pakhomo la hema wake.+ 11 Pamenepo Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake+ Yoswa, mwana wa Nuni,+ sanali kuchoka m’chihemacho, popeza anali kalinde.

12 Tsopano Mose anauza Yehova kuti: “Inu mukundiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa,’ koma simunandidziwitse amene mudzam’tuma kuti ndiyende naye limodzi. Komanso mwanena kuti ‘Ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe,+ ndipo ndakukomera mtima.’ 13 Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ chonde ndidziwitseni njira zanu,+ kuti ndikudziweni, kutinso mundikomere mtima. Ndipo kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”+ 14 Pamenepo Mulungu anati: “Ineyo ndidzayenda nawe+ ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”+ 15 Zitatero iye anati: “Ngati inuyo simuyenda nafe, musatichotse pano. 16 Ndipo ndidziwa bwanji kuti mwandikomera mtima, ineyo ndi anthu anu? Si mwa kuyenda nafe kodi?+ Pajatu ine ndi anthu anu mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+

17 Chotero Yehova anatinso kwa Mose: “Ndidzachita izinso zimene wanena,+ chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.” 18 Pamenepo Mose anati: “Ndionetseni ulemerero wanu.”+ 19 Koma Mulungu anati: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse,+ ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.+ Amene ndikufuna kum’komera mtima ndidzam’komera mtima, ndipo amene ndikufuna kum’sonyeza chifundo, ndidzam’sonyeza chifundo.”+ 20 Ndipo anawonjezera kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angandione n’kukhalabe ndi moyo.”+

21 Ndiyeno Yehova ananenanso kuti: “Nawa malo pafupi ndi ine, ndipo ukakhale pathanthwepo. 22 Choncho pamene ulemerero wanga ukudutsa pafupi ndi iwe, ndidzakuika kuphanga la thanthwelo, ndipo ndidzakuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenako ndidzachotsa dzanja langa, ndipo udzaona kumsana kwanga, koma nkhope yanga sudzaiona.”+

34 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+ 2 Ndipo ukonzeke kuti mawa m’mawa ukakwere m’phiri la Sinai ndi kukakhala pafupi ndi ine kumeneko, pamwamba pa phirilo.+ 3 Koma usakwere m’phirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo.+ Kuwonjezera apo, nkhosa kapena ng’ombe zisadye m’tsinde mwa phirilo.”+

4 Chotero Mose anasemadi miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka m’mamawa ndi kukwera m’phiri la Sinai, atanyamula miyala iwiriyo m’manja mwake, monga momwe Yehova anam’lamulira. 5 Pamenepo Yehova anatsika+ mumtambo ndi kuimirira pafupi ndi Mose, n’kulengeza dzina lake lakuti Yehova.+ 6 Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+ 7 Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+

8 Nthawi yomweyo, Mose anagwada n’kuweramira pansi.+ 9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+ 10 Poyankha Mulungu anati: “Tsopano ndichita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zinthu zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena m’mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzachita nanu chinthu chochititsa mantha.+

11 “Koma inu sungani zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 12 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu a m’dziko limene mukupitako+ kuopera kuti ungakhale msampha pakati panu.+ 13 Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati yawo yopatulika mukaidule.+ 14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+ 15 Samalani, kuopera kuti mungachite pangano ndi anthu okhala m’dzikomo, pakuti iwo adzachita chiwerewere ndi milungu yawo+ ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.+ Chifukwa mukachita nawo pangano, mosakayikira wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+ 16 Kenako mudzatenga ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna,+ ndipo ana awo aakazi adzachita chiwerewere ndi milungu yawo, n’kuchititsa ana anu aamuna kuchita chiwerewere ndi milungu yawo.+

17 “Musadzipangire milungu ya mafano opangidwa ndi chitsulo chosungunula.+

18 “Muzisunga chikondwerero cha mkate wosafufumitsa.+ Monga momwe ndinakulamulirani, muzidya mkate wosafufumitsa masiku 7 m’mwezi wa Abibu*+ pa nthawi yoikidwiratu, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi wa Abibu.

19 “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga,+ ngakhalenso mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, ng’ombe ndi nkhosa.+ 20 Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa.+ Koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi. Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine ali chimanjamanja.+

21 “Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzisunga sabata.+ M’nyengo yolima ndi m’nyengo yokolola muzisunga sabata.+

22 “Muzichita chikondwerero cha masabata ndi tirigu woyamba kucha pa nyengo yokolola tiriguyo.+ Muzichitanso chikondwerero cha zokolola kumapeto kwa chaka.+

23 “Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azionekera+ kwa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli. 24 Pakuti ndidzathamangitsira mitunduyo kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakuza dera lanu.+ Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.+

25 “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chofufumitsa.+ Ndipo nsembe ya chikondwerero cha pasika isamagone mpaka m’mawa.+

26 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa+ za m’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.”+

27 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Dzilembere mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+ 28 Choncho Mose anakhalabe m’phirimo ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Mawu Khumi,* pamiyala yosemayo.+

29 Ndiyeno Mose anatsika m’phiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ija ya Umboni m’manja mwake,+ koma iye sanadziwe kuti nkhope yake inali kuwala chifukwa anali atalankhula ndi Mulungu.+ 30 Aroni ndi ana onse a Isiraeli ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala, ndipo anaopa kumuyandikira.+

31 Pamenepo Mose anawaitana. Chotero Aroni ndi atsogoleri onse a khamu la Isiraeli anabwerera kwa iye, ndipo Mose anayamba kulankhula nawo. 32 Kenako ana onse a Isiraeli anamuyandikira, ndipo iye anayamba kuwauza malamulo onse amene Yehova anam’patsa paphiri la Sinai.+ 33 Mose akatha kulankhula nawo anali kuika chophimba pankhope yake.+ 34 Koma Mose akamalowa kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, anali kuchotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako anali kupita kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza zimene walamulidwa.+ 35 Ndipo ana a Isiraeli anali kuona kuti nkhope ya Mose ikuwala.+ Choncho Mose anali kuphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+

35 Kenako Mose anaitana khamu lonse la ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula kuti muzichita:+ 2 Muzigwira ntchito masiku 6,+ koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse. Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+ 3 Pa tsiku la sabata, musayatse moto m’malo anu alionse okhala.”

4 Pamenepo Mose anauza msonkhano wonse wa ana a Isiraeli kuti: “Yehova walamula kuti, 5 ‘Nonse mupereke zopereka kwa Yehova.+ Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa+ apereke kwa Yehova zinthu monga golide, siliva, mkuwa,+ 6 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ubweya wa mbuzi.+ 7 Aperekenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe, 8 mafuta a nyale, mafuta a basamu opangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ 9 miyala ya onekisi, miyala yozika pa efodi*+ ndi pachovala pachifuwa.+

10 “‘Onse aluso+ pakati panu abwere ndi kupanga zinthu zonse zimene Yehova walamula. 11 Zinthu zimenezo ndizo chihema chopatulika ndi chophimba chake, ngowe zake, mafelemu ake, mipiringidzo yake, nsanamira zake ndi zitsulo zake zokhazikapo mafelemu ndi mizati. 12 Apangenso likasa+ ndi mitengo yake yonyamulira,+ chivundikiro,+ nsalu yotchinga,+ 13 tebulo+ ndi zipangizo zake zonse ndi mitengo yake yonyamulira, mkate wachionetsero,+ 14 choikapo nyale+ zounikira ndi zipangizo zake, nyale zake, ndi mafuta+ a nyalezo. 15 Apangenso guwa lansembe zofukiza+ ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga pakhomo la chihema chopatulika, 16 guwa lansembe+ zopsereza ndi sefa wake wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni+ ndi choikapo chake. 17 Apange nsalu za mpanda wa bwalo,+ mizati yake ndi zitsulo zake zokhazikapo mizatiyo, nsalu yotchinga chipata cha bwalolo, 18 zikhomo za chihema chopatulika, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake.+ 19 Apangenso zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo opatulika, zovala zopatulika+ za Aroni wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.’”

20 Pamenepo msonkhano wonse wa ana a Isiraeli unachoka pamaso pa Mose. 21 Kenako aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa,+ komanso, aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa, anabwera ndipo anabweretsa zopereka kwa Yehova zoti zikagwire ntchito pachihema chokumanako ndi pa utumiki wonse wochitika pamenepo. Anabweretsanso zinthu zopangira zovala zopatulika. 22 Ndipo anali kubwerabe amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa, amene anapereka nsembe yoweyula* yagolide kwa Yehova. Iwo anabweretsa zokometsera zomanga pazovala, ndolo, mphete, zokongoletsera za akazi, ndi zinthu zosiyanasiyana zagolide.+ 23 Ndipo onse amene anali ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.+ 24 Onse amene anapereka chopereka chasiliva ndi mkuwa anapereka zoperekazo kwa Yehova, ndipo onse amene anali ndi matabwa a mthethe oti akagwire ntchito pa utumiki wonse wa pachihema chopatulika anabwera nawo.

25 Akazi onse aluso+ anawomba nsalu ndi manja awo, ndipo anali kubweretsabe zingwe zopota za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri. 26 Ndipo akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.

27 Atsogoleri anabweretsa miyala ya onekisi ndi miyala yozika pa efodi ndi pachovala pachifuwa,+ 28 mafuta a nyale, mafuta a basamu opangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira.+ 29 Mwamuna ndi mkazi aliyense wofunitsitsa kupereka kenakake ku ntchito zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose, anachita zimenezo. Ana a Isiraeli anabweretsa nsembe yaufulu kwa Yehova.+

30 Kenako Mose anauza ana a Isiraeli kuti: “Yehova waitana ndi kutchula dzina Bezaleli,+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda. 31 Ndipo anam’patsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse. 32 Anam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,+ 33 waluso lolemba pamiyala mochita kugoba ndi wodziwa kupanga mwaluso zinthu zina zilizonse zamatabwa.+ 34 Mulungu waika luso lophunzitsa mumtima mwa Bezaleli ndi mwa Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani. 35 Iye wawapatsa mtima wanzeru+ kuti akhale amisiri aluso pa ntchito zonse za mmisiri wolinganiza kawombedwe ka nsalu+ ndi mmisiri wopeta nsalu ndi ulusi wabuluu. Wawapatsa nzeru zimenezi kutinso achite ntchito za mmisiri wopeta nsalu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ntchito za mmisiri wowomba nsalu. Watero kuti akhale amuna ogwira ntchito ina iliyonse ndi kulinganiza kapangidwe ka zinthu.

36 “Bezaleli komanso Oholiabu+ ndi mwamuna aliyense wa mtima wanzeru amene Yehova wam’patsa nzeru+ ndi kuzindikira+ pa zinthu zimenezi, ayenera kugwira ntchitoyi. Iwowa apatsidwa nzeru ndi kuzindikira kuti adziwe kuchita ntchito zonse zopatulika motsatira zonse zimene Yehova walamula.”+

2 Pamenepo Mose anaitana Bezaleli, Oholiabu ndi mwamuna aliyense wa mtima wanzeru amene Yehova anaika nzeru mumtima mwake.+ Anaitana aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa kugwira ntchitoyi.+ 3 Ndipo iwo anatenga zopereka+ zonse zimene ana a Isiraeli anabweretsa kwa Mose, kuti azigwiritse ntchito pa utumiki wopatulika. Koma ana a Isiraeliwo anapitirizabe kubweretsa kwa Mose nsembe zawo zaufulu tsiku lililonse.

4 Chotero anzeru onse amene anali kuchita ntchito yonse yopatulika anayamba kubwera mmodzimmodzi, kuchokera ku ntchito zawo zimene anali kuchita. 5 Ndipo anauza Mose kuti: “Anthu akubweretsa zinthu zambiri kuposa zimene zikufunikira pa ntchito imene Yehova walamula kuti ichitike.” 6 Chotero Mose analamula kuti alengeze mumsasa wonsewo, kuti: “Abambo ndi amayi, musakonzenso zinthu zina za chopereka chopatulika.” Ndi mawu amenewa, anthu anawaletsa kubweretsa zinthuzo. 7 Choncho zinthuzo zinali zokwanira pa ntchito yonse yoyenera kuchitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikira pa ntchitoyo.

8 Ndipo onse a mtima wanzeru+ amene anali kuchita ntchitoyo anayamba kupanga chihema chopatulika,+ nsalu 10 zopetapo akerubi zophimba chihemacho, zopangidwa ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri. Iye* anapanga zonsezi. 9 M’litali mwake, nsalu iliyonse inali mikono 28, ndipo m’lifupi mwake inali mikono inayi. Nsalu zonse muyezo wake unali wofanana. 10 Nsalu zisanu anazilumikiza,+ ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zinanso zisanu. 11 Kenako anaika zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu imodzi yakumapeto mwa nsalu zolumikizanazo. Anachitanso chimodzimodzi m’mphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi.+ 12 Anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu ina imene inali polumikizirana nsalu ziwirizo. Zingwezo zinakhala moyang’anizana.+ 13 Kenako anapanga ngowe 50 zagolide ndi kulumikiza nsalu ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+

14 Ndiyeno anapanga nsalu za ubweya wa mbuzi zoyala pachihema chopatulika. Anapanga nsalu 11.+ 15 M’litali nsalu iliyonse inali mikono 30, ndipo m’lifupi nsalu iliyonse inali mikono inayi. Nsalu zonse 11 zija muyezo wake unali wofanana.+ 16 Analumikiza nsalu zisanu pazokha, ndi kulumikizanso nsalu 6 pazokha.+ 17 Kenako anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi. Ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu inanso yakumapeto, imene inalumikizana ndi inayo.+ 18 Atatero anapanga ngowe 50 zamkuwa zolumikizira nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi.+

19 Ndiyeno anapanga chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi chophimba chinanso cha pamwamba pake cha chikopa cha akatumbu.+

20 Kenako anapanga mafelemu oimika a chihema chopatulika a matabwa a mthethe.+ 21 M’litali mwake, felemu lililonse linali mikono 10, ndipo m’lifupi mwake felemu lililonse linali mkono umodzi ndi hafu.+ 22 Felemu lililonse linali ndi mano awiri oyandikana. Mafelemu onse a chihema chopatulika anawapanga motero.+ 23 Choncho anapanga mafelemu 20 a chihema chopatulika omangira mbali ya kum’mwera ya chihemacho, yoyang’ana ku Negebu.+ 24 Kenako anapanga zitsulo 40 zasiliva zamphako zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri zokhazikapo felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri zokhazikapo felemu lina la mano awiri.+ 25 Ndipo anapanga mafelemu 20 kuti akhale kumbali inayo ya chihema chopatulika chakumpoto,+ 26 ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali zokhazikapo felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri zokhazikapo felemu lina la mano awiri.+

27 Ndipo kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo, anapangirako mafelemu 6.+ 28 Ndiyeno anapanga mafelemu awiri kuti akhale mizati ya m’makona akumbuyo a chihema chopatulika.+ 29 Ndipo anali ofanana ndi ophatikana kuyambira pansi mpaka pamwamba, pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo amene anali mizati ya m’makona awiri, anawapanga motero.+ 30 Choncho panali mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zinakhala pansi pa felemu limodzi moyandikana ndi zitsulo zinanso ziwiri za felemu lina.+

31 Ndiyeno anapanga mipiringidzo yamtengo wa mthethe, mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali imodzi ya chihema chopatulika,+ 32 ndi mipiringidzo inanso isanu yogwira mafelemu a mbali ina ya chihema chopatulika. Anapanganso mipiringidzo ina isanu yogwira mafelemu a kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo.+ 33 Kenako anapanga mpiringidzo wapakati wogwira mafelemu onse kuyambira kumapeto mpaka kumapeto.+ 34 Ndiyeno anakuta mafelemuwo ndi golide, ndipo anapanga mphete zake zagolide zolowetsamo mipiringidzo. Mipiringidzoyo anaikuta ndi golide.+

35 Kenako anapanga nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi anapetapo akerubi.+ 36 Ndiyeno nsalu imeneyi anaipangira mizati inayi ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyi tinali tagolide. Anapanganso zitsulo zinayi zasiliva zamphako, zokhazikapo mizati imeneyi.+ 37 Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 38 Anapanganso mizati yake isanu ndi tizitsulo take tokolowekapo nsalu yotchingayo. Mitu ya mizatiyo komanso mfundo zake anazikuta ndi golide. Koma zitsulo zake zisanu zamphako zokhazikapo mizatiyo zinali zamkuwa.+

37 Tsopano Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+ 2 Kenako analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+ 3 Ndiyeno analipangira mphete zinayi zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo.+ 4 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+ 5 Mitengo yonyamulirayo anailowetsa m’mphete zam’mbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+

6 Kenako anapanga chivundikiro+ chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+ 7 Anapanganso akerubi awiri agolide. Anali osula ndipo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 8 Kerubi mmodzi anali kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho.+ 9 Mapiko a akerubiwo anali okweza m’mwamba ndi otambasula.+ Iwo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo anakhala moyang’anizana, koma nkhope zawo zinayang’ana pachivundikirocho.+

10 Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe,+ mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+ 11 Analikuta ndi golide woyenga bwino, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+ 12 Analipangiranso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli linazungulira tebulo lonse ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo.+ 13 Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi, mmene munali miyendo yake inayi.+ 14 Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+ 15 Ndiyeno anapanga mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi inali yonyamulira tebulolo.+ 16 Atatero anapanga ziwiya za patebulolo, mbale zake, zikho zake, mitsuko yake ndi mbale zake zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Anazipanga ndi golide woyenga bwino.+

17 Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Chimenechi chinali chosula. Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi m’mbali mwake, ndiponso chinali ndi masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa.+ 18 Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunatuluka nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kunatulukanso nthambi zitatu.+ 19 Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, panalinso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zinali zotero.+ 20 Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa.+ 21 Mfundo imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+ 22 Choikapo nyalecho chinali ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chinali chiwiya chimodzi chosula, chagolide woyenga bwino.+ 23 Ndiyeno anachipangira nyale 7, zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.+ 24 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.*

25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe.+ M’litali mwake linali mkono umodzi, m’lifupi mwake mkono umodzi. Mbali zake zonse zinayi zinali zofanana, ndipo msinkhu wake unali mikono iwiri. Guwalo linali ndi nyanga pamwamba pake.+ 26 Ndiyeno analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi m’mbali mwake kuzungulira guwalo, komanso nyanga zake. Analipangira mkombero wagolide wozungulira guwa lonselo.+ 27 Kumbali ziwiri za guwalo anapangako mphete zagolide, ziwiri kumbali iyi ndi zinanso ziwiri kumbali inayo. Anazipanga m’munsi mwa mkombero kuti muzilowa mitengo yonyamulira guwalo.+ 28 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+ 29 Kuwonjezera pamenepo, anapanganso mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika,+ ndi mafuta onunkhira+ osakaniza mwaluso.

38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza la matabwa a mthethe, m’litali mwake mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake linali mikono itatu.+ 2 Anapanganso nyanga+ m’makona ake anayi. Nyanga zakezo zinatuluka m’makona akewo, ndipo guwalo analikuta ndi mkuwa.+ 3 Kenako anapanga ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. Anapanga ndowa, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko aakulu, ndi zopalira moto. Ziwiya zake zonse anazipanga ndi mkuwa.+ 4 Guwalo analipangiranso sefa wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana. Analowetsa sefayo cha pakati pa guwa lansembe, m’munsi mwa mkombero.+ 5 Analipangiranso mphete zinayi m’makona ake anayi kuti muzilowa mitengo yonyamulira. Mphetezo anazilumikiza pafupi ndi sefa wa zitsulo zamkuwa. 6 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe, ndipo anaikuta ndi mkuwa.+ 7 Mitengoyo anailowetsa m’mphetezo m’mbali mwa guwalo kuti ikhale yonyamulira guwalo.+ Guwa limenelo analipanga ngati bokosi lamatabwa losatseka pansi.+

8 Kenako anapanga beseni losambira lamkuwa+ ndi choikapo chake chamkuwa. Popanga zimenezi anagwiritsa ntchito akalirole* a akazi otumikira, amene anali kutumikira mwadongosolo pachipata cha chihema chokumanako.+

9 Ndiyeno anapanga bwalo la chihema chopatulika.+ Kumbali ya ku Negebu, chakum’mwera, bwalolo analitchinga ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo unali mikono 100 kutalika kwake kumbali imodziyo.+ 10 Nsanamira zake 20 ndi zitsulo 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.+ 11 Kumbali yakumpoto, mpandawo unali mikono 100 kutalika kwake. Nsanamira zake 20 ndi zitsulo 20 zokhazikapo nsanamirazo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.+ 12 Koma kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo unali mikono 50 kutalika kwake. Kunali nsanamira 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo nsanamirazo.+ Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 13 Ndipo kumbali yakum’mawa, kotulukira dzuwa, mpandawo unali mikono 50 kutalika kwake.+ 14 Kumbali imodzi ya chipata cha bwalo, mpanda wa nsaluwo unali mikono 15. Kunali nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+ 15 Ndipo kumbali inanso ya chipata cha bwalolo, mpandawo unali mikono 15 kutalika kwake. Zinali choncho kumbali iyi ya chipata komanso kumbali inayo. Kunali nsanamira zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo nsanamirazo.+ 16 Nsalu zonse za mpanda wotchingira bwalo lonselo zinali za ulusi wopota wabwino kwambiri. 17 Ndipo zitsulo zokhazikapo nsanamira zinali zamkuwa. Tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu za mpanda ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. Mitu ya nsanamirazo inali yokutidwa ndi siliva, ndipo nsanamira zonse za bwalo zinali ndi tizitsulo tasiliva tolumikizira.+

18 Ndiyeno nsalu yotchinga pachipata cha bwalo inali yowombedwa mwaluso. Anaiwomba ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Inali mikono 20 kutalika kwake, ndipo nsalu yonseyo msinkhu wake unali mikono isanu, mofanana ndi nsalu zotchingira mpanda wa bwalo.+ 19 Mizati yake inayi ndi zitsulo zinayi zokhazikapo mizatiyo zinali zamkuwa. Tizitsulo ta mizatiyo tokolowekapo nsalu tinali tasiliva, ndipo mitu ya mizatiyo ndi tizitsulo tolumikizira anazikuta ndi siliva. 20 Zikhomo zonse za chihema chopatulika ndi za bwalo lonse zinali zamkuwa.+

21 Tsopano izi ndiye zinthu zonse zimene anawerengera za chihema chopatulika, chihema cha Umboni,+ monga mwa ntchito ya Alevi,+ motsogoleredwa ndi Itamara+ mwana wa Aroni wansembe. Iwo anawerengera zimenezi Mose atalamula. 22 Bezaleli+ mwana wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda, anachita zonse zimene Yehova analamula Mose. 23 Iye anali ndi Oholiabu,+ mwana wa Ahisama wa fuko la Dani, mmisiri wa ntchito zosiyanasiyana, katswiri wodziwa kupeta ndi wodziwa kuwomba nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.

24 Golide yense amene anagwiritsidwa ntchito pa ntchito yonse ya pamalo oyera, anali woperekedwa monga nsembe yoweyula.*+ Muyezo wake unali matalente 29 ndi masekeli 730 pamuyezo wolingana ndi sekeli+ la kumalo oyera.*+ 25 Ndipo siliva wa anthu amene anawerengedwa m’khamu la Isiraeli, anali matalente 100 ndi masekeli 1,775 pamuyezo wolingana ndi sekeli la kumalo oyera. 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+

27 Matalente 100 asiliva anawagwiritsa ntchito kupangira zitsulo zamphako za malo oyera zokhazikapo mafelemu ndi zitsulo zamphako za pafupi ndi nsalu yotchinga. Anagwiritsa ntchito matalente 100 kupangira zitsulo 100 zamphako, talente imodzi anapangira chitsulo chimodzi.+ 28 Masekeli 1,775 asiliva anawagwiritsa ntchito kupangira tizitsulo ta nsanamira tokolowekapo nsalu, ndi kukutira mitu ya nsanamirazo. Atatero analumikiza nsanamirazo.

29 Mkuwa wa nsembe yoweyula unali matalente 70 ndi masekeli 2,400. 30 Ndipo mkuwa umenewu anaugwiritsa ntchito kupangira zitsulo zamphako zokhazikapo mizati ya pakhomo la chihema chokumanako, guwa lansembe lamkuwa, sefa wa guwalo wa zitsulo zolukanalukana ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. 31 Anapangiranso zitsulo zokhazikapo nsanamira za mpanda wa bwalo lonse, zitsulo zokhazikapo mizati ya pachipata cha bwalolo, zikhomo+ zonse za chihema chopatulika ndi zikhomo zonse za bwalo.

39 Ndiyeno anapanga zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo oyera,+ pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri.+ Motero anapanga zovala zopatulika+ za Aroni, monga mmene Yehova analamulira Mose.

2 Kenako anapanga efodi*+ wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. 3 Ndiyeno anasula golide kukhala wopyapyala kwambiri, ndipo anam’lenzalenza kukhala ngati tizingwe kuti apetere limodzi ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wabwino kwambiri.+ 4 Anapanganso nsalu za m’mapewa zolumikiza ku efodiyo. Anazilumikiza pamapewa. 5 Lamba womangira efodi, wolumikiza ku efodiyo anali wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Anali wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

6 Ndiyeno anakonza miyala ya onekisi+ ndi kuiika m’zoikamo zagolide. Pamiyalayo analembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+ 7 Ndipo miyalayo anailowetsa pansalu za m’mapewa za efodi kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana a Isiraeli, monga mmene Yehova analamulira Mose. 8 Kenako anapanga chovala pachifuwa+ ndipo anachipanga mwaluso mofanana ndi efodi. Chinali chagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 9 Akachipinda pakati chinali chofanana mbali zonse zinayi. Chovala pachifuwacho anachipanga kuti akachipinda pakati, m’litali mwake chizikhala chikhatho* chimodzi ndipo m’lifupi mwake chikhatho chimodzi.+ 10 Ndiyeno pachovala pachifuwacho anaikapo mizere inayi ya miyala. Mzere woyamba unali ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi.+ 11 Mzere wachiwiri+ unali ndi miyala ya nofeki, safiro+ ndi yasipi.+ 12 Mzere wachitatu+ unali ndi miyala ya lesemu, sibu ndi ametusito. 13 Ndipo mzere wa chinayi+ unali ndi miyala ya kulusolito, onekisi+ ndi yade. Anaiika m’zoikamo zake zagolide. 14 Miyalayo anaiika malinga ndi mayina a mafuko a ana a Isiraeli, ndipo inalipo 12, malinga ndi mayina awo. Mwala uliwonse analembapo mochita kugoba limodzi mwa mayina a mafuko 12, ngati mmene amagobera chidindo.+

15 Ndipo pachovala pachifuwa anapangapo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota mwaluso.+ 16 Anapanganso zoikamo miyala ziwiri zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anaika mphete ziwirizo m’makona awiri a chovala pachifuwacho.+ 17 Kenako anapisa zingwe ziwiri zagolide zija m’mphete ziwiri za m’makona a chovala pachifuwa.+ 18 Ndipo anamangirira zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri. Kenako anaika zoikamo miyala ziwirizo pansalu za m’mapewa za efodi, chapatsogolo pake.+ 19 Atatero anapanga mphete ziwiri zagolide ndi kuziika m’makona awiri a chovala pachifuwa, kumbali yopindira mkati yokhudzana ndi efodi.+ 20 Ndiyeno anapanga mphete ziwiri zagolide ndi kuziika pansalu ziwiri za pamapewa za efodi m’munsi mwake, kutsogolo kwa nsaluzo, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba wa efodi.+ 21 Atatero anamanga chovala pachifuwacho ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chinalowa m’mphete za chovala pachifuwa ndi mphete za efodi, kuti chovala pachifuwacho chizikhala pamwamba pa lamba wa efodi, kutinso chisasunthe pa efodipo, monga mmene Yehova analamulira Mose.+

22 Ndiyeno anapanga malaya odula manja+ ovala mkati mwa efodi, a nsalu yowomba ndi ulusi wabuluu wokhawokha. 23 Ndipo malaya odula manjawo anali otsegula pamwamba pake, pakatikati, ngati chovala cha kunkhondo chamamba achitsulo. Potsegulapo panali popenderera m’mphepete mwake kuti pasang’ambike.+ 24 Mumpendero wake wa m’munsi anapangamo makangaza a ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri, wopota pamodzi.+ 25 Kenako anapanganso mabelu agolide woyenga bwino ndi kuwaika pakati pa makangaza,+ kuzungulira mpendero wa m’munsi wa malaya odula manjawo, pakati pa makangaza. 26 Anaika belu ndi khangaza,* belu ndi khangaza, kuzungulira mpendero wa m’munsi mwa malaya odula manja.+ Malayawo ndi oti azivala potumikira, monga mmene Yehova analamulira Mose.

27 Kenako anawomba mikanjo ya Aroni ndi ana ake ya ulusi wabwino kwambiri.+ 28 Ndiyeno anapanga nduwira+ ya nsalu yabwino kwambiri, mipango yokongola yokulunga kumutu+ ya nsalu zabwino kwambiri ndi makabudula a nsalu+ za ulusi wopota wabwino kwambiri. 29 Anawombanso lamba wa pamimba+ ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri, monga mmene Yehova analamulira Mose.

30 Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Chiyero n’cha Yehova.”+ Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo. 31 Ndiyeno analowetsa chingwe chabuluu m’kachitsuloko kuti akamangirire panduwirayo,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

32 Chotero ntchito yonse ya chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, inatha, chifukwa ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.+ Anachitadi momwemo.

33 Pamenepo anabweretsa kwa Mose chihema chopatulika+ ndi zipangizo zake zonse,+ nsalu yake yophimba pamwamba,+ ngowe zake,+ mafelemu ake,+ mitengo yake yonyamulira,+ mizati yake ndi zitsulo zamphako zoika pansi.+ 34 Anabweretsanso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto+ wofiira, chophimba chinanso cha pamwamba pake cha chikopa cha akatumbu,+ nsalu yotchinga,+ 35 likasa+ la umboni, mitengo yake yonyamulira,+ chivundikiro chake,+ 36 tebulo,+ ziwiya zake zonse+ ndi mkate wachionetsero. 37 Anabweretsanso choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, nyale zake zondandalikidwa bwino,+ ziwiya zonse za choikapo nyalecho,+ mafuta a nyale,+ 38 guwa lansembe+ lagolide, mafuta odzozera,+ zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la chihemacho, 39 guwa lansembe+ lamkuwa, sefa wake wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana,+ mitengo yake yonyamulira,+ ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo,+ beseni losambira+ ndi choikapo chake.+ 40 Anabweretsanso nsalu zotchingira+ bwalo, mizati+ ndi zitsulo zokhazikapo mizatiyo,+ nsalu yotchinga+ pachipata cha bwalo, zikhomo za bwalo+ ndi zingwe zogwira mpanda,+ ziwiya zonse+ zogwiritsa ntchito pa utumiki wa pachihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, 41 zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo opatulika, zovala zopatulika+ za Aroni wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.+

42 Ana a Isiraeli anachita utumiki wonse motsatira zonse zimene Yehova analamulira Mose.+ 43 Ndipo Mose ataona ntchito yonse, anaona kuti achita zonse monga mmene Yehova analamulira. Iwo anachitadi momwemo. Pamenepo Mose anawadalitsa.+

40 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 2 “Mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo,+ udzautse chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako.+ 3 Mkati mwake, udzaikemo likasa la umboni+ ndi kutchinga kumene kuli Likasalo ndi nsalu.+ 4 M’chihemacho udzaikemonso tebulo+ ndi kuikapo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemonso choikapo nyale+ ndi kuyatsa nyale zake.+ 5 Ndiyeno udzaike guwa lansembe lagolide la zofukiza,+ patsogolo pa likasa la umboni, ndi kuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema chopatulika.+

6 “Udzaike guwa lansembe+ zopsereza patsogolo pa khomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako. 7 Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe, ndi kuthiramo madzi.+ 8 Kenako udzatchinge bwalo+ la chihema chopatulika ndi mpanda, ndipo pachipata cha bwalolo udzakolowekepo nsalu yake yotchinga.+ 9 Ndiyeno udzatenge mafuta odzozera+ ndi kudzoza chihema chopatulika ndi zonse zimene zili mkati mwake.+ Motero udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10 Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse ndi kuliyeretsa.+ Pamenepo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.+ 11 Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake ndi kuliyeretsa.

12 “Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako, ndi kuwalamula kuti asambe ndi madzi.+ 13 Ukatero, udzaveke Aroni zovala zopatulika,+ kenako um’dzoze+ ndi kumuyeretsa kuti atumikire monga wansembe wanga. 14 Ndiyeno udzatenge ana ake ndi kuwaveka mikanjo.+ 15 Ndipo udzawadzoze ngati mmene wadzozera abambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo adzatumikirabe monga ansembe odzozedwa m’mibadwo yawo yonse mpaka kalekale.”+

16 Pamenepo Mose anachita zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+ Anachitadi momwemo.

17 Choncho m’mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anautsa chihema chopatulika.+ 18 Pamene Mose anali kuutsa chihema chopatulikacho, anayala pansi zitsulo zake zamphako+ ndi kukhazikapo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa mitengo yake yonyamulira+ ndi kuimika mizati pamalo ake.+ 19 Atatero anayala nsalu yophimba pachihemacho+ ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, monga mmene Yehova analamulira Mose.

20 Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa mitengo yonyamulira+ m’mbali mwa Likasalo ndi kuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21 Pamenepo analowetsa Likasa m’chihema chopatulika ndi kuika nsalu yotchinga+ pamalo ake, kutchinga likasa la umboni,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

22 Ndiyeno analowetsa tebulo+ m’chihema chokumanako, n’kuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa nsalu yotchinga. 23 Kenako anasanja mkate woonetsa+ Yehova patebulopo, monga mmene Yehova analamulira Mose.

24 Atatero analowetsa choikapo nyale+ m’chihema chokumanako ndi kuchiika patsogolo pa tebulo, kumbali yakum’mwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.

26 Kenako analowetsa guwa lansembe lagolide+ m’chihema chokumanako, ndi kuliika patsogolo pa nsalu yotchinga, 27 kuti azifukizirapo zofukiza zonunkhira,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

28 Atatero anakoloweka nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema chopatulika.

29 Ndiyeno anaika guwa lansembe+ zopsereza pakhomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, monga mmene Yehova analamulira Mose.

30 Kenako pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe anaikapo beseni n’kuthiramo madzi osamba.+ 31 Mose, Aroni ndi ana ake anali kusamba m’manja ndi m’mapazi awo pamenepo. 32 Akamalowa m’chihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe anali kusamba,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

33 Atatero anatchinga mpanda+ kuzungulira bwalo la chihema chopatulika ndi guwa lansembe, ndipo anakoloweka nsalu yotchinga pachipata cha bwalolo.+

Chotero Mose anamaliza ntchitoyo. 34 Pamenepo mtambo+ unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho. 35 Mose sanathenso kulowa m’chihema chokumanako, chifukwa mtambo+ unaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+

36 M’zigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukakwera pamwamba pa chihema chokumanako, ana a Isiraeli anali kunyamuka n’kuyamba ulendo.+ 37 Koma ukapanda kukwera, iwo sanali kunyamuka mpaka tsiku limene wakwera.+ 38 Mtambo wa Yehovawo unali kukhala pamwamba pa chihema chopatulika usana, ndipo usiku panali kukhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inali kuona zimenezi m’zigawo zonse za ulendo wawo.+

M’mizinda imeneyi anamangamo nkhokwe ndi nyumba zina zosungiramo chakudya ndi zinthu zina.

Zimenezi zinali njerwa zosawotcha.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 35:17.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Dzinali limatanthauza “Wovuulidwa; Wopulumutsidwa M’madzi.”

Dzinali limatanthauza “Wokhala Monga Mlendo Kumeneko.”

Yetero amatchedwanso kuti Reueli. Onani Eks 2:18.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “Ineyo ndidzakhala ndi pakamwa pako komanso pakamwa pake.”

Mawu ake enieni, “Ndine wosadulidwa milomo,” ngati kuti milomo yake inali ndi khungu lolendewera, moti inali yaitali kwambiri ndi yochindikala, yomulepheretsa kulankhula bwinobwino.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.

Mawu ake enieni, “tirigu ndi sipeloti.” Sipeloti ndi mtundu wa tirigu koma wosakoma ngati tirigu weniweni. Anthu a ku Iguputo kalekalelo anali kulima mbewuyi.

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda, kuyambira pamene iwo anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.

Mawu ake enieni, “pakati pa madzulo awiri.” Malinga n’kunena kwa akatswiri ena, komanso Ayuda achikaraite ndi Asamariya, nthawi imeneyi ikuyambira pamene dzuwa lalowa kufikira pamene mdima weniweni wagwa. Koma Afarisi ndi Arabi ali ndi maganizo osiyana ndi amenewa. Iwo amati, madzulo oyamba ndi pamene dzuwa layamba kupendeka, ndipo madzulo achiwiri ndi kulowa kwa dzuwa kwenikweniko.

M’chinenero choyambirira, mawu omwe tawamasulira kuti “pasika” amatanthauza “kulumpha,” kapena “kupitirira.”

Kapena kuti “ng’ombe zazing’ono.”

Mawu ake enieni, “Ndiyeno kukhala kwa ana a Isiraeli, amene anakhala m’dziko la Iguputo.” Mabaibulo ena akale amasonyeza kuti chiwerengero cha zaka chimene chatchulidwachi sichikuimira zaka zimene Aisiraeli anakhala mu Iguputo mokha ayi, komanso chikuphatikizapo zaka zimene anakhala ku Kanani.

Mawu ake enieni, “Munthu amene si Mwisiraeli.”

Mawu ake enieni, “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa, wotsegula mimba ya mayi aliyense.”

Onani Zakumapeto 13.

Mawu ake enieni, “pakati pa maso anu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu akuti “dzanja lokwezeka” akutanthauza kuti ana a Isiraeli anatuluka mosonyeza mphamvu, kulimba mtima ndi kupambana.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Aheberi ankagawa usiku m’magawo atatu, ndipo uwu unali ulonda wachitatu komanso womaliza. Unali kuyamba cha m’ma 2 koloko usiku mpaka 6 koloko m’mawa.

M’Baibulo lonse, mawu akuti “Ya” akutchulidwa koyamba pavesi lino. Mawu amenewa ndi chidule cha dzina lakuti “Yehova,” ndipo ndi mbali yoyamba ya zilembo zinayi zoimira dzina lenileni la Mulungu, lakuti YHWH. Onani Zakumapeto 2.

Dzinali limatanthauza “Kuwawa.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.

Muyezo wa “omeri” limodzi ndi wofanana ndi chitini cha malita awiri.

Zikuoneka kuti dzinali limatanthauza kuti “N’chiyani ichi?” Onani vesi 15.

Mawu ake enieni, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.

Kapena kuti “Chikumbutso.” Zikuoneka kuti limeneli linali bokosi losungiramo zolembalemba zofunika.

“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

“Horebe.” Dzinali silikutanthauza phiri limene analandirirapo Malamulo Khumi koma dera lamapiri ambiri lozungulira phiri la Sinai. Derali limadziwikanso ndi dzina lakuti chipululu cha Sinai.

Dzinali likutanthauza kuti “Kuyesa,” kapena kuti “Chiyeso.”

Dzinali likutanthauza kuti “Kukangana; Ndewu,” kapena “Mikangano.”

Mawu ake enieni, “Yehoswa,” kutanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso”; Chigiriki, Ἰησοῦ (I·e·souʹ, “Yesu”).

“Padziko lapansi.” Mawu ake enieni, “pansi pa thambo.”

Zikuoneka kuti dzinali limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Chizindikiro Changa.”

Kutanthauza kuti “Ndi Mlendo Kumeneko.”

Kutanthauza kuti “Mulungu Wanga Ndi Mthandizi.”

Kapena kuti “anapereka.”

Zikuoneka kuti mawu amenewa akutanthauza tsiku limene ananyamuka ku Refidimu.

Apa akunena za kugonana.

Kapena kuti “motsutsana ndi ine.”

Mawu ake enieni, “madzi a pansi pa dziko,” mwina chifukwa chakuti nyanja ndi mitsinje zimakhala pamalo olowa poyerekeza ndi mtunda.

Kapena kuti “Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.

Kapena kuti “nsembe zamtendere,” kutanthauza nsembe zosonyeza kuti woperekayo ali pa mtendere ndi Mulungu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Kutanthauza kuti, kupita naye kwa oweruza oimira Mulungu woona.

Mwina chifukwa cha kusasamala kapena chifukwa cha zochitika zina zimene akanatha kuzipewa.

“Chiwongo” ndi ndalama zimene mwamuna amalipira pokwatira. Ena amati “chimalo.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

“Ngongole yakatapira” ndi ngongole imene munthu pobweza amayenera kuwonjezerapo ndalama zina zochuluka. Ena amati “kalowa.”

Onani Zakumapeto 13.

Mawu ake enieni, “Ndidzakupatsa kumbuyo kwa makosi a adani ako onse.”

Mabaibulo a Septuagint ndi Vulgate amanena kuti, “ndidzatumizira anthuwo mavu.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Katumbu ndi nyama yaubweya ya m’madzi, ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka m’nyanja zikuluzikulu.

Zikuoneka kuti chimenechi chinali chovala chofanana ndi epuloni, ndipo chinali ndi nsalu yakutsogolo ndi yakumbuyo. Onani Zakumapeto 14.

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

“Chikhatho” chimenechi chinali muyezo wokwana masentimita 7.4.

“Talente limodzi” limalemera makilogalamu pafupifupi 34.2.

Kapena kuti “chihema chokumanako ndi Mulungu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.

Umenewu ndi utali wofanana ndi utali wochokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kudutsa pakati pa chikhatho chanu, kukafika pansonga ya chala chaching’ono, mutatambasula chikhatho. Utali umenewu ndi wokwana masentimita 22.2.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

M’Chiheberi mawu amenewa kwenikweni amatanthauza “kudzaza manja,” ndipo amatchulidwa ponena za kupatsa mphamvu zonse anthu oti azitumikira monga ansembe.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.

“Chiwindi” ena amati “mphafa.”

Mawu ake enieni, “kuzifukiza.”

Mawu akuti “kuweyula” akutanthauza kunyamula chinthu n’kuchiyendetsa mbali iyi ndi mbali inayo.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.

“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.

“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 16:34.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.

Kapena kuti “lolingana ndi sekeli lopatulika.” Umenewu unali muyezo wachikhalire umene anali kuusunga m’chihema chopatulika. N’kutheka kuti mawu akuti “lolingana ndi sekeli la kumalo oyera” anali kungotsindika kuti muyezowo uyenera kukhala wokwanira bwino. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa 2Sa 14:26.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Sitakate” ndi utomoni wonunkhira wa mitengo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “masikiyo.”

Mawu ake enieni “dzazani manja anu ndi mphamvu.”

Kapena kuti “Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”

Onani Zakumapeto 13.

Mawu akuti “Mawu Khumi” akutanthauza mawu khumi olamula, zinthu khumi zoyenera kuchita, kapena Malamulo Khumi.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:5.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

“Iye” akuimira Bezaleli.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:25.

“Talente limodzi” linali kulemera makilogalamu pafupifupi 34.2.

Amenewa anali akalirole achitsulo amene anali kuwasalalitsa kwambiri kuti azionetsa nkhope.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 30:13.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:16.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:33.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena