Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Leviticus 1:1-27:34
  • Levitiko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Levitiko
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Levitiko

Levitiko

1 Tsopano kuchokera m’chihema chokumanako,+ Yehova anaitana Mose ndi kulankhula naye kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli+ kuti, ‘Munthu aliyense akafuna kupereka chiweto kwa Yehova kuti ikhale nsembe, azipereka ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi.

3 “‘Ngati akupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza,+ azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako. 4 Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa+ kuti iphimbe machimo ake.+

5 “‘Kenako azipha ng’ombe yaing’onoyo pamaso pa Yehova. Ndiyeno ana a Aroni, ansembe,+ azibweretsa magazi ake ndi kuwawaza mozungulira paguwa lansembe,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako. 6 Nyama ya nsembe yopserezayo aziisenda chikopa ndi kuidula ziwaloziwalo.+ 7 Pamenepo ana a Aroni, ansembe, aziika moto paguwa lansembelo+ ndi kuyalapo nkhuni.+ 8 Ndipo ana a Aroni, ansembe, aziyala ziwalozo+ pankhuni zimene zili pamoto wa paguwa lansembepo. Aziyala ziwalozo pamodzi ndi mutu ndiponso mafuta. 9 Matumbo+ ake ndi ziboda zake azizitsuka ndi madzi. Akatero ansembe azitentha* nyama yonse paguwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+

10 “‘Ngati akupereka nkhosa+ kapena mbuzi kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka+ mwana wamphongo wopanda chilema.+ 11 Ndipo aziipha pamaso pa Yehova kumbali yakumpoto ya guwa lansembe. Akatero ana a Aroni, ansembe, aziwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe.+ 12 Kenako azidula nyamayo ziwaloziwalo. Azichotsa mafuta ake ndi mutu wake ndipo wansembe aziyala ziwalo zonsezo pankhuni zimene zili pamoto wa paguwa lansembepo.+ 13 Ndiyeno azitsuka matumbo+ ndi ziboda+ ndi madzi. Kenako wansembe azitenga nyama yonseyo ndi kuitentha+ paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+

14 “‘Koma ngati akupereka mbalame kuti ikhale nsembe yake yopsereza kwa Yehova, azipereka njiwa+ kapena ana a nkhunda.+ 15 Wansembe azibweretsa mbalameyo paguwa lansembe ndi kudula*+ mutu wake. Akatero aziitentha paguwa lansembe, koma magazi ake aziwakhetsera pansi pambali pa guwa lansembelo. 16 Azichotsa chitsokomero ndi nthenga zake ndi kuziponya potayira phulusa losakanizika ndi mafuta,+ chakum’mawa, pafupi ndi guwa lansembe. 17 Ndiyeno aziing’amba pakati cham’mapiko mwake, koma osailekanitsa.+ Kenako wansembe aziitentha paguwa lansembe pamwamba pa nkhuni zimene zili pamoto. Imeneyi ndi nsembe yopsereza,+ nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+

2 “‘Munthu akafuna kupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, nsembe yakeyo izikhala ufa wosalala.+ Azithira mafuta ndi kuika lubani* pa ufawo. 2 Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, ndi kuutentha paguwa lansembe kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 3 Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake,+ popeza ndi zopatulika koposa,+ zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.

4 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati,+ wopanda chofufumitsa, wothira mafuta, kapena timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa,+ topaka mafuta.+

5 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika m’chiwaya,+ izikhala ya ufa wabwino kwambiri wothira mafuta, yopanda chofufumitsa. 6 Muziibenthula zidutswazidutswa ndi kuithira mafuta.+ Imeneyi ndi nsembe yambewu.

7 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mumphika wa mafuta ambiri, izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala ndiponso mafuta. 8 Ndipo nsembe yambewu yopangidwa moteremu muzibwera nayo kwa Yehova. Muziipereka kwa wansembe, ndipo iye azipita nayo paguwa lansembe. 9 Kenako wansembe azitengako pang’ono nsembe yambewu kuti ikhale chikumbutso,+ ndipo azitentha zimene watengazo paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 10 Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake, popeza ndi zopatulika koposa zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+

11 “‘Nsembe yambewu imene mudzapereka kwa Yehova ikhale yopanda chofufumitsa,+ chifukwa simuyenera kutentha mtanda wofufumitsa wa ufa wokanda ndiponso uchi,* monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

12 “‘Zimenezi mudzazipereka kwa Yehova monga nsembe ya zipatso zoyambirira,+ chotero simuyenera kuzibweretsa paguwa lansembe kuti zikhale nsembe yafungo lokhazika mtima pansi.

13 “‘Nsembe yanu iliyonse yambewu muziikoleretsa ndi mchere.+ Musapereke nsembe yanu yambewu yopanda mchere wokukumbutsani pangano+ la Mulungu. Popereka nsembe yanu iliyonse muziperekanso mchere.

14 “‘Ngati mukupereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha,+ muzipereka tirigu* wamuwisi wotibula, wokazinga pamoto, kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha. 15 Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu.+ 16 Ndipo wansembe azitentha chikumbutso+ cha nsembeyo, kapena kuti, tirigu wotibula uja pang’ono ndi mafuta, pamodzi ndi lubani wake yense, kuti zikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

3 “‘Ngati akupereka nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, ndipo akufuna kupereka ng’ombe yamphongo kapena yaikazi, azipereka yopanda chilema.+ 2 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu+ pa ng’ombeyo, ndipo aziipha pakhomo la chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, ansembe, aziwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe. 3 Pamenepo azipereka mbali ina ya nsembe yachiyanjanoyo monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. Azipereka mafuta+ okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+ 4 Aziperekanso impso ziwiri+ ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi,* aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 5 Kenako ana a Aroni+ azitentha+ zinthu zimenezi paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni+ zimene zili pamoto. Imeneyi ikhale nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi+ kwa Yehova.

6 “‘Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yachiyanjano kwa Yehova, azipereka yamphongo kapena yaikazi, yopanda chilema.+ 7 Ngati akupereka nkhosa yaing’ono yamphongo monga nsembe yake, aziipereka kwa Yehova.+ 8 Pamenepo aziika dzanja lake pamutu+ pa nkhosayo, ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero, ana a Aroni aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe. 9 Ndipo pansembe yachiyanjanoyo azitengapo mafuta ake ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto.+ Azichotsa mchira wonse wamafuta+ pafupi ndi fupa la msana ndiponso mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+ 10 Azichotsanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta+ a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 11 Ndipo wansembe azitentha+ zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya,+ kuti chikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

12 “‘Ngati akupereka mbuzi+ monga nsembe yake, aziibweretsa pamaso pa Yehova. 13 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa mbuziyo,+ ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe. 14 Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo,+ ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto. 15 Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 16 Ndipo wansembe azitentha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi. Mafuta onse ndi a Yehova.+

17 “‘Musamadye mafuta kapena magazi+ alionse. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale,* kulikonse kumene mungakhale.’”

4 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu+ akachimwa mosadziwa+ mwa kuchita zinthu zimene Yehova analamula kuti musachite, iye akachita chimodzi mwa zimenezo muzichita izi:

3 “‘Ngati wansembe, wodzozedwa,+ wachita tchimo+ limene lapalamulitsa anthu onse, azipereka kwa Yehova ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+ 4 Azibweretsa ng’ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova pakhomo la chihema chokumanako+ ndipo aziika dzanja lake pamutu wa ng’ombeyo,+ kenako aziipha pamaso pa Yehova. 5 Pamenepo wansembe, wodzozedwayo,+ azitengako pang’ono magazi a ng’ombeyo ndi kulowa nawo m’chihema chokumanako. 6 Kenako wansembe aziviika chala chake+ m’magaziwo ndi kudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7+ pamaso pa Yehova, patsogolo pa nsalu yotchinga ya m’malo oyera. 7 Wansembeyo azipaka ena mwa magaziwo panyanga+ za guwa lansembe la zofukiza zonunkhira pamaso pa Yehova, limene lili m’chihema chokumanako. Magazi ena onse a ng’ombeyo aziwathira pansi+ pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pakhomo la chihema chokumanako.

8 “‘Koma mafuta onse a ng’ombe ya nsembe yamachimo, aziwachotsa. Azichotsa mafuta okuta matumbo, mafuta onse okuta matumbo.+ 9 Azichotsanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+ 10 Zinthu zimenezi zizikhala zofanana ndi zomwe azichotsa pa ng’ombe ya nsembe yachiyanjano.+ Ndipo wansembe azizitentha paguwa lansembe zopsereza.+

11 “‘Koma kunena za chikopa cha ng’ombeyo ndi nyama yake yonse pamodzi ndi mutu wake, ziboda zake, matumbo ake ndi ndowe zake,+ 12 ng’ombe yonseyo aziitenga ndi kupita nayo kunja kwa msasa.+ Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa losakanizika ndi mafuta+ ndipo aziitentha pamoto wa nkhuni.+ Azitentha ng’ombeyo kumalo otayako phulusa losakanizika ndi mafuta.

13 “‘Tsopano ngati khamu lonse la Isiraeli lachita cholakwa,+ mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite ndipo chawapalamulitsa, koma mpingo wonse sunazindikire kuti walakwa,+ 14 ndipo tchimo limene achitalo ladziwika,+ pamenepo mpingowo uzipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo monga nsembe yamachimo, azibwera nayo pakhomo la chihema chokumanako. 15 Kumeneko akulu a khamu la Isiraeli aziika manja awo pamutu wa ng’ombeyo+ pamaso pa Yehova, ndipo aziipha pamaso pa Yehova.

16 “‘Pamenepo wansembe, wodzozedwa,+ azibweretsa ena mwa magazi a ng’ombeyo m’chihema chokumanako.+ 17 Ndipo wansembe aziviika chala chake m’magaziwo ndi kuwadontheza pansi maulendo 7 pamaso pa Yehova, patsogolo pa nsalu yotchinga.+ 18 Ena mwa magaziwo aziwapaka panyanga za guwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova, m’chihema chokumanako. Magazi ena onse aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako. 19 Akatero azichotsa mafuta ake onse ndi kuwatentha paguwa lansembe.+ 20 Ng’ombeyo azichita nayo ngati mmene amachitira ndi ng’ombe ya nsembe yamachimo ija. Azichita momwemo. Ndipo wansembe aziwaphimbira machimo+ awo kuti akhululukidwe. 21 Azitenganso ng’ombe ndi kukaitentha kunja kwa msasa monga mmene anatenthera ng’ombe yoyamba ija.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo ya mpingo wonse.+

22 “‘Ngati mtsogoleri+ wachimwa mwa kuchita mwangozi chimodzi mwa zinthu zimene Yehova Mulungu wake analamula kuti asachite+ ndipo wapalamula, 23 kapena ngati wauzidwa kuti wachimwa mwa kuphwanya lamulo,+ azibweretsa mbuzi yaing’ono yamphongo,+ yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yake. 24 Akatero aziika dzanja lake pamutu+ pa mbuzi yaing’onoyo ndipo aziipha pamaso pa Yehova,+ pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse. Imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 25 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimoyo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 26 Mafuta onse a mbuziyo aziwatentha paguwa lansembe mofanana ndi mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe aziphimba tchimo la mtsogoleriyo,+ ndipo azikhululukidwa.

27 “‘Ngati munthu aliyense pakati panu wachimwa mwa kuchita mwangozi chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite ndipo wapalamula,+ 28 kapena ngati wauzidwa kuti wachimwa, azibweretsa mbuzi yaing’ono yaikazi,+ yopanda chilema, kuti ikhale nsembe chifukwa cha machimo akewo. 29 Akatero aziika dzanja lake pamutu+ pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo azipha nyamayo pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza aja.+ 30 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe+ zopsereza. 31 Kenako azichotsa mafuta onse+ a mbuziyo, monga mmene amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe azitentha mafutawo paguwa lansembe kuti likhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo, ndipo azikhululukidwa.+

32 “‘Koma ngati akubweretsa nkhosa+ monga nsembe yake yamachimo, azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi yopanda chilema.+ 33 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo aziipha kuti ikhale nsembe yamachimo, pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse.+ 34 Wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza.+ Magazi ena onse a nkhosayo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 35 Ndiyeno azichotsa mafuta onse a nkhosayo, monga mmene amachotsera mafuta a nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe yachiyanjano. Pamenepo wansembe azitentha zinthu zimenezi paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ Ndipo wansembe aziphimba+ tchimo limene munthuyo wachita, ndipo azikhululukidwa.+

5 “‘Tsopano munthu+ akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo,+ munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo* kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena,+ ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.

2 “‘Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta, kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake,+ iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.+ 3 Munthu akakhudza mosadziwa chodetsa chilichonse chochokera kwa munthu,+ chinthu chilichonse chodetsedwa chimene chingam’chititse kukhala wodetsedwa, koma wadziwa kuti wakhudza chodetsa, pamenepo wapalamula mlandu.

4 “‘Munthu akalumbira mpaka kulankhula mosalingalira bwino,+ mwa kunena kuti achita choipa+ kapena chabwino, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, koma akadziwa kuti walankhula mosalingalira bwino pa chilichonse chimene walumbira,+ pamenepo wapalamula mlandu pa chimene walumbiracho.

5 “‘Ndipo akadziwa kuti wapalamula mlandu pa chilichonse mwa zimenezi, pamenepo aziulula+ kuti wachimwa motani. 6 Ndiyeno azibweretsa kwa Yehova nsembe yake ya kupalamula+ chifukwa cha tchimo limene wachita. Azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi+ kapena mbuzi yaing’ono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.+

7 “‘Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa,+ azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda kuti zikhale nsembe za kupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo+ ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 8 Pamenepo azizibweretsa kwa wansembe, ndipo wansembeyo azipereka nsembe yamachimo choyamba, ataicheka+ pakhosi koma osaduliratu mutu wake. 9 Kenako azidontheza ena mwa magazi a nsembe yamachimo m’mbali mwa guwa lansembe, koma magazi otsalawo aziwathira pansi pa guwa lansembelo.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Mbalame inayo aziipereka ngati nsembe yopsereza motsatira ndondomeko ya nthawi zonse.+ Choncho wansembe aziphimba machimo+ amene munthuyo wachita, ndipo azikhululukidwa.+

11 “‘Koma ngati sangakwanitse+ kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*+ Azibweretsa ufa umenewu monga nsembe yake chifukwa cha tchimo limene anachitalo, kuti ukhale nsembe yamachimo. Asauthire mafuta+ ndipo asaikemo lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 12 Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Kenako autenthe paguwa lansembe pamene pali nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 13 Ndiyeno wansembeyo aziphimba+ tchimo limene munthuyo wachita. Aziphimba tchimo lililonse mwa machimo amenewa, ndipo azikhululukidwa. Ufa wotsalawo uzikhala wa wansembe+ mofanana ndi nsembe yambewu.’”

14 Pamenepo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 15 “Munthu akachita mosakhulupirika mwa kuchimwira zinthu zopatulika za Yehova+ mosadziwa, pamenepo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake ya kupalamula.+ Nkhosayo mtengo wake uzikhala masekeli* asiliva+ ofanana ndi sekeli la kumalo oyera* kuti ikhale nsembe ya kupalamula. 16 Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera azilipira mwa kubweza zinthu zopatulikazo ndiponso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a malipirowo. Malipirowo aziwapereka kwa wansembe, ndipo mwa kupereka nkhosa ya nsembe ya kupalamula, wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo azikhululukidwa.+

17 “Munthu akachimwa mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira,+ komabe wapalamula mlandu, pamenepo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ 18 Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene wachita mosadziwa, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, ndipo azikhululukidwa.+ 19 Imeneyi ndi nsembe ya kupalamula. Munthu ameneyo wapalamula mlandu+ kwa Yehova.”

6 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Munthu akachimwa mwa kuchita mosakhulupirika kwa Yehova+ chifukwa wanyenga+ mnzake pa chinthu chimene chili m’manja mwake, kapena chimene mnzake wam’sungitsa,+ kapena wafwamba mnzake, kapena wam’bera mwachinyengo,+ 3 kapena watola chinthu chotayika+ koma akukana kuti sanachitole, ndipo walumbira monama+ pa chilichonse chimene munthu angachite n’kuchimwa nacho, 4 iye akachimwa mwa njira imeneyi, ndipo wapalamuladi,+ azibweza zinthu zimene anafwambazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene chili m’manja mwake chimene anam’sungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola, 5 kapena chilichonse chimene angalumbirire monama. Azibweza+ chinthucho ndi kuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake asanu. Iye azibweza zimenezi kwa mwiniwake, tsiku limene kulakwa kwake kwatsimikizidwa. 6 Monga nsembe yake ya kupalamula, azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema.+ Azipereka kwa wansembe nkhosa ya mtengo wofanana ndi mtengo umene wagamulidwa, kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+ 7 Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo azikhululukidwa chilichonse mwa zonse zimene angachite zom’palamulitsa.”

8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 9 “Lamula Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza+ lili motere: Nsembe yopsereza izikhala pamoto, paguwa lansembe, usiku wonse kufikira m’mawa, ndipo moto wa paguwapo uzisonkhezeredwa. 10 Ndiyeno wansembe azivala zovala zake zogwirira ntchito,+ ndi kuvala kabudula wansalu+ wobisa thupi lake. Kenako azichotsa phulusa losakanizika ndi mafuta,+ la nsembe yopsereza imene izitenthedwa pamoto wa paguwa nthawi zonse, ndipo aziika phulusalo pambali pa guwa lansembe. 11 Ndiyeno azivula zovalazo+ ndi kuvala zina. Akatero, azitenga phulusa losakanizika ndi mafutalo kupita nalo kumalo oyera, kunja kwa msasa.+ 12 Ndipo moto wa paguwa lansembe uziyaka nthawi zonse. Usamazime. Wansembe aziponyapo nkhuni+ m’mawa uliwonse ndi kuikapo nsembe yopsereza pankhunipo. Akatero, azitentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamotopo.+ 13 Motowo+ uziyaka nthawi zonse paguwa lansembe. Usamazime.

14 “‘Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ lili motere: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi, ndi kutengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, azizitentha paguwa lansembe kuti zikhale fungo la chikumbutso,+ lokhazika mtima pansi, kwa Yehova. 16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda chofufumitsa+ ndi kudya mkatewo m’malo oyera. Aziudyera m’bwalo la chihema chokumanako. 17 Pophika, musaikemo chofufumitsa chilichonse.+ Ndaupereka monga gawo lawo kuchokera pansembe zanga zotentha ndi moto.+ Zimenezi n’zopatulika+ koposa mofanana ndi nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula. 18 Mwamuna aliyense+ mwa ana a Aroni azidya mkatewo. Limeneli ndi gawo lawo lochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.+ Chilichonse chimene chingakhudze nsembezi chidzakhala choyera.’”

19 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 20 “Aroni ndi ana ake apereke nsembe+ iyi kwa Yehova monga nsembe yambewu: ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ Hafu imodzi m’mawa ndipo hafu inayo madzulo. Aliyense wa iwo azichita zimenezi nthawi zonse pa tsiku la kudzozedwa kwake.+ 21 Nsembeyo ikhale yosakaniza ndi mafuta, yophika m’chiwaya.+ Ikhale yosakaniza bwino ndi mafuta. Upereke mitanda ya nsembe yambewu monga fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 22 Ndipo wansembe, amene adzadzozedwa kulowa m’malo mwake, wochokera pakati pa ana ake,+ azipereka nsembeyo. Azitentha nsembe yonseyo kuti ikhale nsembe+ yoperekedwa kwa Yehova. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 23 Nsembe iliyonse yambewu ya wansembe+ izitenthedwa yonse. Siiyenera kudyedwa.”

24 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 25 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yamachimo+ lili motere: Nyama ya nsembe yamachimo iziphedwa pamaso pa Yehova, pamalo+ ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse. Chimenechi ndi chinthu chopatulika koposa.+ 26 Wansembe amene waipereka monga nsembe yamachimo aziidya.+ Aziidyera kumalo oyera,+ m’bwalo+ la chihema chokumanako.

27 “‘Chilichonse chimene chingakhudze mnofu wake chidzakhala choyera,+ ndipo ngati munthu wadonthezera ena mwa magazi a nyamayo pachovala,+ chovala chimene wadonthezera magazicho muzichichapira kumalo oyera.+ 28 Ndipo chiwiya chadothi+ chimene mungawiritsiremo nyamayo muzichiswa. Koma mukawiritsira m’chiwiya chamkuwa, muzichikwecha ndi kuchitsukuluza ndi madzi.

29 “‘Mwamuna aliyense amene ndi wansembe azidya nyamayo.+ Ndi yopatulika koposa.+ 30 Koma musadye nyama ya nsembe yamachimo imene ena mwa magazi+ ake adzalowa nawo m’chihema chokumanako kuti aphimbire machimo m’malo oyerawo. Imeneyo muziitentha ndi moto.

7 “‘Lamulo la nsembe ya kupalamula+ lili motere: Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+ 2 Nyama ya nsembe ya kupalamula aziiphera pamalo+ amene nthawi zonse amaphera nyama ya nsembe yopsereza, ndipo magazi ake+ aziwazidwa+ mozungulira paguwa lansembe. 3 Pa mafuta ake onse+ azipereka mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo. 4 Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+ 5 Ndipo wansembe azitentha zinthu zimenezi paguwa lansembe monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe ya kupalamula. 6 Mwamuna aliyense yemwe ndi wansembe azidya nyamayo.+ Azidyera m’malo oyera. Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+ 7 Nsembe ya kupalamula ndi yofanana ndi nsembe yamachimo. Zonsezi lamulo lake ndi limodzi.+ Nyama ya nsembe yophimba machimo izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo.

8 “‘Chikopa+ cha nyama ya nsembe yopsereza, imene munthu aliyense wapereka kwa wansembe, chizikhala cha wansembe amene wapereka nsembeyo.

9 “‘Nsembe iliyonse yambewu imene ingaphikidwe mu uvuni,+ iliyonse yophika mu mphika wa mafuta ambiri+ ndiponso yophika m’chiwaya+ izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo. Ndithu izikhala yake.+ 10 Koma nsembe yambewu iliyonse yothira mafuta+ kapena youma+ izikhala ya ana onse aamuna a Aroni, azigawana mofanana.

11 “‘Tsopano lamulo la nsembe yachiyanjano+ imene aliyense azipereka kwa Yehova lili motere: 12 Ngati akupereka nsembeyo posonyeza kuyamikira,+ pamenepo azipereka nsembe yoyamikira pamodzi ndi mkate wozungulira woboola pakati, wopanda chofufumitsa, wothira mafuta. Aziperekanso timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa, topaka mafuta,+ ndi mkate wozungulira woboola pakati, wothira mafuta, wophika ndi ufa wosalala wosakaniza bwino kwambiri ndi mafuta. 13 Popereka nsembe zachiyanjano, zimene ndi nsembe yoyamikira pamodzi ndi nsembe yake ya mkate, aziperekanso makeke okhala ndi chofufumitsa,+ ozungulira oboola pakati. 14 Ndipo pa zimenezi azipereka mtanda umodzi wa nsembe iliyonse kuti ikhale gawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova.+ Mtandawo uzikhala wa wansembe+ amene wawaza magazi a nsembe zachiyanjanozo paguwa lansembe. 15 Nyama ya nsembe zachiyanjano zoperekedwa monga nsembe yoyamikira aziidya pa tsiku limene waipereka. Asasunge iliyonse ya nyamayo kufika m’mawa.+

16 “‘Ngati akupereka lonjezo+ monga nsembe yake kapena ngati akupereka nsembe yaufulu,+ aziidya pa tsiku limene wapereka nsembeyo, ndipo angathenso kudya imene yatsala pa tsiku lotsatira. 17 Nyama ya nsembeyo, imene yatsala kufika tsiku lachitatu, ayenera kuitentha ndi moto.+ 18 Koma ngati nyama iliyonse ya nsembe yachiyanjano yadyedwa pa tsiku lachitatu, wopereka nsembeyo sadzayanjidwa ndi Mulungu.+ Nsembe yakeyo sadzapindula nayo.+ Idzakhala chinthu chonyansa, ndipo amene wadyako nsembeyo adzadziyankhira mlandu wa cholakwa chake.+ 19 Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa,+ siyenera kudyedwa. Muziitentha ndi moto. Koma nyama imene sinadetsedwe, aliyense woyera angathe kuidya.

20 “‘Munthu amene wadya nyama ya nsembe yachiyanjano, imene ndi ya Yehova, pamene munthuyo ali wodetsedwa, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 21 Ndipo munthu akakhudza chodetsa chilichonse, kaya chodetsa cha munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ n’kudyako nyama ya nsembe yachiyanjano, imene ndi ya Yehova, munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”

22 Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 23 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Musamadye mafuta+ alionse a ng’ombe, a mwana wa nkhosa, kapena a mbuzi. 24 Mafuta a nyama yofa yokha ndi mafuta a nyama yokhadzulidwa ndi chilombo,+ mungawagwiritse ntchito ina iliyonse imene mungafune, koma musawadye ngakhale pang’ono. 25 Pakuti aliyense wodya mafuta a nyama imene waipereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto, munthu ameneyo aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.

26 “‘Musamadye magazi+ alionse kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama. 27 Munthu aliyense wodya magazi alionse aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”

28 Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 29 “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu amene akupereka nsembe yake yachiyanjano kwa Yehova, azipereka kwa Yehova mbali ya nsembe yake yachiyanjanoyo.+ 30 Iye azibweretsa mafuta+ pamodzi ndi nganga monga nsembe kwa Yehova yotentha ndi moto. Azibweretsa mafutawo pamodzi ndi nganga kuti aziweyule* uku ndi uku, monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova. 31 Ndiyeno wansembe azitentha mafutawo+ paguwa lansembe, koma ngangayo izikhala ya Aroni ndi ana ake.+

32 “‘Mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja muziupereka kwa wansembe monga gawo lopatulika+ lochokera pansembe zanu zachiyanjano. 33 Mwana wa Aroni amene wapereka kwa Mulungu magazi a nsembe zachiyanjano ndiponso mafuta, azitenga mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja monga gawo lake.+ 34 Nganga ya nsembe yoweyula+ ndiponso mwendo, umene ndi gawo lopatulika, ndikuzitenga pansembe zachiyanjano za ana a Isiraeli. Ndikuzitenga kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Ili ndi lamulo mpaka kalekale.

35 “‘Limeneli ndilo linali gawo la Aroni monga wansembe ndiponso gawo la ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa+ kuti atumikire monga ansembe a Yehova. 36 Pa tsiku lopatula Aroni ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli ndi kuwadzoza,+ Yehova analamula kuti adzawapatse gawoli. Ili ndi lamulo m’mibadwo yawo yonse mpaka kalekale.’”+

37 Limeneli ndilo lamulo lokhudza nsembe yopsereza,+ nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo,+ nsembe ya kupalamula,+ nyama yoperekedwa polonga munthu unsembe+ ndiponso nsembe yachiyanjano,+ 38 monga mmene Yehova analamulira Mose paphiri la Sinai,+ pa tsiku limene analamula ana a Isiraeli kupereka nsembe zawo kwa Yehova m’chipululu cha Sinai.+

8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Tenga Aroni pamodzi ndi ana ake,+ zovala zawo,+ mafuta odzozera,+ ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo,+ nkhosa ziwiri zamphongo, ndi dengu la mikate yopanda chofufumitsa.+ 3 Ndiyeno usonkhanitse khamu lonse+ pakhomo la chihema chokumanako.”+

4 Mose anachita monga mmene Yehova anam’lamulira. Ndipo khamu lonse linasonkhana pakhomo+ la chihema chokumanako. 5 Pamenepo Mose anauza khamulo kuti: “Yehova walamula kuti tichite zinthu izi.”+ 6 Kenako Mose anaitana Aroni ndi ana ake ndi kuwalamula kuti asambe.+ 7 Atatero anaveka Aroni mkanjo+ ndi kum’manga lamba wa pamimba.+ Anamuvekanso malaya odula manja+ komanso efodi,*+ ndi kum’manga kwambiri ndi lamba+ wa efodiyo. 8 Anamuveka chovala cha pachifuwa+ ndi kuika Urimu ndi Tumimu+ m’chovala cha pachifuwacho. 9 Anamuvekanso nduwira+ pamutu pake, n’kuika patsogolo pa nduwirayo kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

10 Ndiyeno Mose anatenga mafuta odzozera n’kudzoza chihema chopatulika+ ndi zonse zimene zinali mkati mwake, n’kuzipatula. 11 Anawaza ena mwa mafuta odzozerawo maulendo 7 paguwa lansembe+ ndi kudzoza guwa lansembelo, zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake, n’kuzipatula. 12 Pomalizira, Mose anathira ena mwa mafuta odzozera pamutu pa Aroni ndi kum’dzoza kuti akhale wopatulika.+

13 Kenako Mose anaitana ana a Aroni+ ndi kuwaveka mikanjo, kuwamanga malamba a pamimba,+ ndi kuwakulunga mipango+ kumutu, monga mmene Yehova analamulira Mose.

14 Atatero anabweretsa ng’ombe yamphongo+ ya nsembe yamachimo, ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu+ pa ng’ombe ya nsembe yamachimoyo. 15 Ndiyeno Mose anapha+ ng’ombeyo, ndipo anatenga magazi+ ake ndi kuwapaka ndi chala chake panyanga zonse za guwa lansembe, n’kuyeretsa guwalo ku uchimo. Koma magazi otsalawo anawathira pansi pa guwa lansembe kuti alipatule, kuphimba machimo+ paguwalo. 16 Ndipo Mose anatenga mafuta onse okuta matumbo, mafuta a pachiwindi ndi impso ziwiri ndi mafuta ake, n’kuzitentha paguwa lansembe.+ 17 Koma chikopa cha ng’ombeyo, nyama yake ndi ndowe zake anazitentha kunja kwa msasa,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.

18 Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 19 Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe.+ 20 Atatero anaidula ziwaloziwalo,+ ndipo Mose anatenga mutu wake, ziwalozo ndi mafuta ake, ndi kuziika paguwa lansembe. 21 Anatenganso matumbo ndi ziboda n’kuzitsuka ndi madzi. Ndiyeno Mose anatentha nkhosa yonseyo paguwa lansembe.+ Inali nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi.+ Komanso, inali nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.

22 Atatero anabweretsa nkhosa yamphongo yachiwiri, nkhosa yolongera unsembe,+ ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo. 23 Mose anapha nkhosayo ndi kutengako magazi ake n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la Aroni, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha kumwendo wa kudzanja lamanja.+ 24 Kenako Mose anaitana ana a Aroni ndi kuwapaka magazi m’munsi pakhutu lawo la kudzanja lamanja, pachala chawo chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chawo chachikulu cha kumwendo wa kudzanja lamanja. Koma Mose anawaza magazi otsalawo mozungulira paguwa lansembe.+

25 Pamenepo anatenga mafuta a nkhosayo, mchira wa mafuta, mafuta onse okuta matumbo,+ mafuta a pachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja.+ 26 M’dengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta,+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala.+ Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja. 27 Atatero anaika zonsezi m’manja mwa Aroni ndi m’manja mwa ana ake n’kuyamba kuziweyula* uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ 28 Ndiyeno Mose anazitenga m’manja mwawo n’kuzitentha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza.+ Zimenezi zinali nsembe yowalongera unsembe,+ yafungo lokhazika mtima pansi.+ Inali nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+

29 Kenako Mose anatenga nganga+ ndi kuiweyula uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ Nganga imeneyi anaitenga pa nkhosa yowalongera unsembe ndipo inakhala gawo+ la Mose, monga mmene Yehova analamulira Mose.

30 Atatero Mose anatengako mafuta odzozera+ ndi magazi amene anali paguwa lansembe aja n’kuwawaza pa Aroni ndi pazovala zake. Anawawazanso pa ana ake aja ndi pazovala zawo. Motero anapatula+ Aroni ndi zovala zake komanso ana a Aroni+ ndi zovala zawo.

31 Ndiyeno anauza Aroni ndi ana ake kuti: “Wiritsani+ nyamayo pakhomo la chihema chokumanako, ndipo muidyerenso pomwepo+ pamodzi ndi mkate umene uli m’dengu logwiritsidwa ntchito polonga anthu unsembe, monga mmene anandilamulira, kuti, ‘Aroni ndi ana ake adye zimenezi.’ 32 Ndipo nyama ndi mkate zotsala muzitenthe ndi moto.+ 33 Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kwa masiku 7,+ kufikira tsiku lomaliza la kulongedwa kwanu unsembe, chifukwa kukupatsani mphamvu* kudzatenga masiku 7.+ 34 Yehova walamula kuti mmene zachitikira lero, zichitikenso chimodzimodzi pa masiku otsalawa pokuphimbirani machimo.+ 35 Chotero mukhale pakhomo la chihema chokumanako usana ndi usiku kwa masiku 7.+ Ndipo muyenera kuchita ulonda umene Yehova walamula,+ kuti musafe. Chifukwa n’zimene ndalamulidwa.”

36 Choncho Aroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.

9 Tsopano pa tsiku la 8,+ Mose anaitana Aroni, ana ake ndi akulu a Isiraeli. 2 Pamenepo anauza Aroni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Nyama zonsezi zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke kwa Yehova.+ 3 Koma uza ana a Isiraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yamphongo+ kuti ikhale nsembe yamachimo. Mutengenso mwana wa ng’ombe ndi nkhosa yaing’ono yamphongo,+ zonsezi zikhale za chaka chimodzi, zopanda chilema, kuti zikhale nsembe yopsereza. 4 Mutengenso ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo kuti muzipereke kwa Yehova monga nsembe zachiyanjano.+ Komanso mubwere ndi nsembe yambewu+ yothira mafuta, chifukwa lero Yehova aonekera ndithu kwa inu.’”+

5 Choncho anthuwo anatenga zimene Mose analamula n’kupita nazo kuchihema chokumanako. Kenako khamu lonse linayandikira ndi kuima pamaso pa Yehova.+ 6 Ndiyeno Mose anati: “Mverani zimene Yehova walamula kuti muchite, kuti ulemerero wa Yehova uonekere kwa inu.”+ 7 Pamenepo Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo+ ako ndi a nyumba yako. Kenako uperekere nsembe anthuwa+ ndi kuwaphimbira machimo awo,+ monga mmene Yehova walamulira.”

8 Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe ndi kupha ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yake yamachimo.+ 9 Ndiyeno ana ake anam’bweretsera magazi+ a ng’ombeyo, ndipo iye anaviika chala chake m’magaziwo+ ndi kuwapaka panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo. 10 Ndipo mafuta,+ impso ndi mafuta a pachiwindi zimene anazitenga panyama ya nsembe yamachimo anazitentha paguwa lansembe,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 11 Koma nyama ndi chikopa chake anazitentha kunja kwa msasa.+

12 Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza, ndipo ana ake anam’patsa magazi a nyamayo. Pamenepo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+ 13 Kenako anam’patsa ziwalo za nyama ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu, ndipo anazitentha paguwa lansembe.+ 14 Atatero, anatsuka matumbo ndi ziboda, n’kuzitentha paguwa lansembe+ pamwamba pa nsembe yopsereza.

15 Ndiyeno anaperekera nsembe anthu.+ Anatenga mbuzi yoperekera anthu nsembe yamachimo, ndipo anaipha, n’kuipereka monga nsembe yamachimo, mmene anachitira ndi nyama yoyamba ija. 16 Atatero anapereka nsembe yopsereza motsatira ndondomeko yake.+

17 Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake ndi kuitentha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya m’mawa.+

18 Ndiyeno Aroni anapha ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yachiyanjano yoperekera anthuwo.+ Kenako ana ake anam’patsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+ 19 Kunena za mafuta+ a ng’ombeyo, mchira wa mafuta+ wa nkhosa, mafuta okuta matumbo, impso ndi mafuta a pachiwindi, 20 ana a Aroni anaika zinthu za mafuta zimenezo pamwamba pa nganga+ za nyamazo. Kenako anatentha mafutawo paguwa lansembe. 21 Koma Aroni anaweyula*+ cha uku ndi uku ngangazo ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja pamaso pa Yehova, monga mmene Mose analamulira.

22 Kenako Aroni anakweza manja ake pa anthuwo ndi kuwadalitsa.+ Atatero, anatsika+ kuguwa lansembe kumene anali atapereka nsembe yamachimo, nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano. 23 Pamenepo Mose ndi Aroni analowa m’chihema chokumanako, kenako anatulukamo n’kudalitsa anthuwo.+

Atatero, ulemerero wa Yehova+ unaonekera kwa anthu onse, 24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ n’kunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi, anayamba kufuula mokondwera+ ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.

10 Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira,+ n’kuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Pamenepo anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule. 2 Atatero, moto unatsika kuchokera kwa Yehova ndi kuwawononga,+ moti anafa pamaso pa Yehova.+ 3 Chotero Mose anauza Aroni kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Anthu amene ali pafupi ndi ine+ ayenera kundiona kukhala woyera,+ ndipo anthu onse azindipatsa ulemerero.’”+ Pamenepo Aroni anangokhala chete.

4 Zitatero, Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli,+ bambo aang’ono a Aroni, n’kuwauza kuti: “Bwerani muchotse abale anu patsogolo pa malo oyera, mupite nawo kunja kwa msasa.”+ 5 Iwo anabweradi ndi kuwanyamula osawavula mikanjo yawo n’kupita nawo kunja kwa msasa, monga mmene Mose ananenera.

6 Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara, kuti: “Musalekerere tsitsi lanu osalisamala,+ ndipo musang’ambe zovala zanu kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire khamu lonseli.+ Abale anu, nyumba yonse ya Isiraeli ndiwo alire chifukwa cha kuwononga ndi moto kumene Yehova wachita. 7 Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kuopera kuti mungafe,+ chifukwa mwadzozedwa ndi mafuta odzozera a Yehova.”+ Choncho iwo anachita monga mwa mawu a Mose.

8 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: 9 “Pamene mukubwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa,+ kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, 10 kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa ndiponso pakati pa chodetsedwa ndi choyera.+ 11 Kutinso muziphunzitsa ana a Isiraeli+ malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzera mwa Mose.”

12 Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso ndi Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, kuti: “Tengani nsembe yambewu+ imene yatsala pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda chofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe, chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+ 13 Mudye nsembeyo m’malo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi n’zimene ndalamulidwa. 14 Mudyenso nganga ya nsembe yoweyula,*+ ndi mwendo umene ndi gawo lopatulika.+ Muzidyere m’malo oyera, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muyenera kutero chifukwa zapatsidwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zachiyanjano za ana a Isiraeli. 15 Iwo azibweretsa mwendo wa gawo lopatulika ndi nganga ya nsembe yoweyula,+ pamodzi ndi mafuta a nsembe zotentha ndi moto, kuti woperekayo aziweyule uku ndi uku pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala gawo lanu+ ndi gawo la ana anu mpaka kalekale, monga mmene Yehova walamulira.”

16 Ndiyeno Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yamachimo,+ koma anaona kuti yonse inali itatenthedwa pamoto. Pamenepo iye anakwiyira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, ndipo anati: 17 “N’chifukwa chiyani simunadye nsembe yamachimo m’malo oyera?+ Nsembe imeneyi ndi yopatulika koposa, ndipo Mulungu wakupatsani kuti munyamule zolakwa za khamu lonse, ndi kuphimba machimo a khamu lonseli pamaso pa Yehova.+ 18 Taonani, simunabweretse magazi ake mkati, m’malo oyera.+ Munafunika kudya nsembeyo m’malo oyera, monga mmene Mulungu anandilamulira.”+ 19 Pamenepo, Aroni analankhula ndi Mose kuti: “Lerotu apereka nsembe yawo yamachimo ndi nsembe yawo yopsereza kwa Yehova,+ pamene zinthu izi zikundigwera. Kodi ndikanati ndadya nsembe yamachimo lero, zikanakhala zokhutiritsa pamaso pa Yehova?”+ 20 Mose atamva zimenezi, zinam’khutiritsa.

11 Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Uzani ana a Isiraeli kuti, ‘Zolengedwa zimene mungadye+ pa nyama zonse zimene zili padziko lapansi ndi izi: 3 Cholengedwa chilichonse pakati pa nyama, chimene chili ndi ziboda zogawanika zokhala ndi mpata pakati, chomwenso chimabzikula, n’chimene mungadye.+

4 “‘Koma pakati pa nyama zimene zimabzikula ndi zimene zili ndi ziboda zogawanika, izi zokha musadye: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake n’zosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+ 5 Ndiponso mbira,+ chifukwa imabzikula, koma ziboda zake n’zosagawanika. Ikhale yodetsedwa kwa inu. 6 Chimodzimodzinso kalulu,+ chifukwa amabzikula, koma ziboda zake n’zosagawanika. Akhale wodetsedwa kwa inu. 7 Komanso nkhumba,+ chifukwa ziboda zake n’zogawanika ndipo zili ndi mpata pakati, koma siibzikula. Ikhale yodetsedwa kwa inu. 8 Musadyeko nyama iliyonse ya zimenezi, ndipo nyamazi zikafa musamazikhudze.+ Zikhale zodetsedwa kwa inu.+

9 “‘Zimene mungadye pa zonse za m’madzi ndi izi: Chilichonse cha m’madzi+ chokhala ndi zipsepse ndi mamba,+ chopezeka m’nyanja ndi m’mitsinje mungadye. 10 Koma pa zamoyo za m’madzi zopezeka zambiri ndi pa zamoyo zina zonse za m’madzi, chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba, chopezeka m’nyanja ndi m’mitsinje, chikhale chonyansa kwa inu. 11 Zinthu zimenezi zikhale zonyansa kwa inu. Musamadye nyama yake iliyonse,+ ndipo zikafa zizikhalabe zonyansa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse cha m’madzi chimene chilibe zipsepse ndi mamba, chikhale chonyansa kwa inu.

13 “‘Pakati pa zolengedwa zouluka,+ izi zikhale zonyansa kwa inu. Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: Chiwombankhanga,+ nkhwazi ndi muimba wakuda. 14 Komanso mtundu uliwonse wa mphamba wofiira ndi mphamba wakuda,+ 15 ndi mtundu uliwonse wa khwangwala.+ 16 Musadyenso nthiwatiwa,+ kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi. 17 Ndiponso musadye nkhwezule, chiswankhono, mantchichi,+ 18 tsekwe, vuwo, muimba,+ 19 dokowe, sadzu, mleme+ ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 20 Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, tikhale tonyansa kwa inu.+

21 “‘Pa tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, mungathe kudya tizilombo tokhalanso ndi miyendo italiitali yolumphira. Tokhati n’timene mungadye. 22 Tizilombo timene mungadyeto ndi iti: Mtundu uliwonse wa dzombe loyenda mitunda italiitali*+ ndi mitundu ina ya dzombe,+ mtundu uliwonse wa nkhululu, ndi mtundu uliwonse wa chiwala.+ 23 Koma tizilombo tina tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, tikhale tonyansa+ kwa inu. 24 Tizilombo timeneti n’timene mungadzidetse nato. Aliyense wokhudza zolengedwa zimenezi zitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 25 Ndipo aliyense wonyamula chilichonse mwa zolengedwa zimenezi chitafa, azichapa+ zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.

26 “‘Nyama iliyonse yokhala ndi chiboda chogawanika koma chosakhala ndi mpata pakati, imenenso siibzikula, ndi yodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza nyama yoteroyo azikhala wodetsedwa.+ 27 Pakati pa zamoyo zonse za miyendo inayi, chamoyo chilichonse chokhala ndi mapazi a zikhadabo n’chodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza chamoyo chimenechi chitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 28 Ndipo munthu wonyamula iliyonse ya nyama zimenezi itafa,+ azichapa zovala zake,+ ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Nyama zimenezi zikhale zodetsedwa kwa inu.

29 “‘Pa zamoyo zonse zokwawa padziko lapansi, zodetsedwa ndi izi:+ Mfuko, mbewa yoyenda modumpha+ ndi mtundu uliwonse wa buluzi. 30 Ndiponso nalimata, buluzi wamkulu, dududu, buluzi wa mumchenga ndi bilimankhwe. 31 Zamoyo zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu pa zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri.+ Aliyense wokhudza zolengedwa zimenezi zitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+

32 “‘Tsopano chamoyo chilichonse mwa zimenezi chikafa n’kugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa. Kaya ndi chiwiya chamtengo,+ chovala, chikopa,+ kapena chiguduli*+ chizikhala chodetsedwa. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziikidwa m’madzi, koma chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo, kenako chizikhala choyera. 33 Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikagwera m’chiwiya chadothi,+ chilichonse chimene chili m’chiwiyacho chizikhala chodetsedwa, ndipo chiwiyacho muzichiphwanya.+ 34 Madzi a m’chiwiya chimenechi akagwera pachakudya chilichonse, chakudyacho chizikhala chodetsedwa. Ndipo chakumwa chilichonse chimene mungamwere m’chiwiya chilichonse, chikasakanikirana ndi madzi ochokera m’chiwiya chodetsedwa chija, chakumwacho chizikhala chodetsedwa. 35 Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikafa n’kugwera pachinthu chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa ndipo chiziphwanyidwa, kaya ndi uvuni kapena chokhazikapo mtsuko. Ziwiya zimenezi zadetsedwa ndipo zikhale zodetsedwa kwa inu. 36 Kasupe ndiponso dziwe ndi zokhazo zimene zizikhalabe zoyera, koma aliyense wokhudza cholengedwa chimene chafacho azikhala wodetsedwa. 37 Ndipo chilichonse mwa zolengedwa zimenezi chikafa n’kugwera pambewu iliyonse yoti mubzale, mbewuyo izikhalabe yoyera. 38 Koma mbewuyo ikathiridwa madzi ndipo chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo n’kugwerapo, mbewuyo izikhala yodetsedwa kwa inu.

39 “‘Nyama iliyonse imene mwaloledwa kudya ikapezeka itafa, aliyense wokhudza nyama yakufayo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 40 Aliyense wakudya+ nyama yofa yokha azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Aliyense wonyamula nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 41 Ndipo zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi zikhale zonyansa.+ Zimenezi musadye. 42 Pa zilombo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi, musamadye chamoyo chilichonse chokwawa+ ndiponso chamoyo chilichonse cha miyendo inayi kapena cha miyendo yambiri, chifukwa zimenezi ndi zonyansa.+ 43 Musamadziipitse ndi zamoyo zilizonse zimene zimapezeka zambirizi ndipo musamadzidetse nazo ndi kukhala odetsedwa.+ 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Mudzipatule ndi kukhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+ Choncho musamadzidetse ndi chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu.+ Muzikhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+

46 “‘Limeneli ndi lamulo lokhudza nyama, zolengedwa zouluka, zamoyo zonse za m’madzi+ ndi zamoyo zonse zapamtunda, 47 kuti muzisiyanitsa+ chodetsedwa ndi choyera komanso zamoyo zimene muyenera kudya ndi zimene simuyenera kudya.’”

12 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mkazi akatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira akamasamba.+ 3 Ndipo pa tsiku la 8, khungu la mwanayo lizidulidwa.+ 4 Kwa masiku enanso 33, mkaziyo azikhala panyumba kuti ayeretsedwe ku magazi ake. Asakhudze chilichonse chopatulika, ndipo asalowe m’malo oyera, kufikira masiku a kuyeretsedwa kwake atakwanira.+

5 “‘Akabereka mwana wamkazi, azikhala wodetsedwa kwa masiku 14. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira akamasamba. Kwa masiku enanso 66 azikhala panyumba kuti ayeretsedwe ku magazi ake. 6 Ndiyeno masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa+ kuti ikhale nsembe yamachimo. 7 Ndipo wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kum’phimbira machimo, pamenepo mkaziyo azikhala woyera pa kukha magazi kwake.+ Limeneli ndi lamulo la mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi. 8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi ikhale nsembe yopsereza, inayo ikhale nsembe yamachimo. Pamenepo wansembe azim’phimbira machimo+ ndipo mkaziyo azikhala woyera.’”

13 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Munthu akatuluka zotupa, kapena nkhanambo,+ kapena chikanga pakhungu lake, ndipo chasintha n’kukhala nthenda ya khate,+ azibwera naye kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake amenenso ndi ansembe.+ 3 Ndiyeno wansembeyo aone nthenda imene yatuluka pakhunguyo.+ Ngati cheya cha pamalopo chasanduka choyera ndipo pakuoneka kuti m’pozama kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe aone nthendayo n’kugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. 4 Koma ngati chikangacho chikuoneka choyera ndipo si chozama kupitirira khungu, komanso cheya sichinasanduke choyera, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku 7. 5 Ndiyeno wansembe azionanso munthuyo pa tsiku la 7, ndipo ngati nthendayo yaoneka kuti yatha, moti sinafalikire pakhungu, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku enanso 7.

6 “Ndiyeno pa tsiku la 7, wansembe azionanso munthuyo kachiwiri. Ngati nthendayo yayamba kuzimiririka ndipo sinafalikire pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Inali chabe nkhanambo. Munthuyo azichapa zovala zake ndi kukhala woyera. 7 Koma ngati nkhanambo yafalikira pakhungu la munthu pambuyo poti anaonekera kwa wansembe ndipo anagamula kuti ndi woyera, munthuyo azikaonekeranso kachiwiri kwa wansembe.+ 8 Pamenepo wansembe azionanso munthuyo, ndipo ngati nkhanambo yake yafalikira pakhungu, wansembeyo azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate.+

9 “Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, azim’bweretsa kwa wansembe. 10 Wansembe aziona nthendayo,+ ndipo ngati pali zotupa moti khungu ndi cheya zayera, ndipo chilondacho chikunyeka,+ 11 limenelo ndi khate losachiritsika+ pakhungu lake, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asam’bindikiritse,+ pakuti ndi wodetsedwa. 12 Koma ngati khate labukadi pakhungu lake, moti n’zoonekeratu kwa wansembe kuti lafalikira pathupi lonse la munthuyo, kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13 ndipo wansembe wamuona, n’kutsimikizira kuti khatelo lafalikiradi thupi lonse, pamenepo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.* Khungu lake lonse latuwa, choncho ndi woyera. 14 Koma tsiku limene zilonda zonyeka zidzaonekera, adzakhala wodetsedwa. 15 Wansembe+ aziona zilondazo ndi kugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha zilondazo. Limenelo ndi khate.+ 16 Kapena ngati zilondazo zapola n’kusanduka zoyera, munthuyo azibwera kwa wansembe. 17 Ndiyeno wansembe azimuona.+ Ngati khungu lake latuwa, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wosadetsedwa. Iye ndi woyera.

18 “Ngati pakhungu la munthu pali chithupsa,+ ndipo kenako chapola, 19 ndipo pamene panali chithupsapo pabuka chotupa choyera kapena chikanga chotuwa mofiirira, munthuyo azikadzionetsa kwa wansembe. 20 Pamenepo wansembe azimuona,+ ndipo ngati chikuoneka kuti n’chozama kupitirira khungu, ndipo cheya chake chasanduka choyera, pamenepo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. Yabuka pachithupsa. 21 Koma wansembe akachiona n’kupeza kuti palibe cheya choyera ndipo si chozama kupitirira khungu komanso chayamba kuzimiririka, pamenepo azim’bindikiritsa+ masiku 7. 22 Ngati chikangacho chafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda. 23 Koma ngati chikangacho sichinasinthe, osafalikira, kumeneko ndi kutukusira+ kwa chithupsa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+

24 “Kapena ngati pakhungu pali chilonda cha moto, ndipo mnofu wa pachilondacho wayamba kuoneka wotuwa mofiirira kapena woyera, 25 pamenepo wansembe aziona chilondacho. Ngati cheya cha pamenepo chasanduka choyera ndipo chilondacho chikuoneka chozama kupitirira khungu, limenelo ndi khate. Labuka pachilonda, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 26 Koma ngati wansembe waona chilondacho, n’kupeza kuti palibe cheya choyera ndipo chilondacho si chozama kupitirira khungu, komanso chikubwerera mwakale, wansembe azim’bindikiritsa masiku 7. 27 Ndipo wansembe aziona munthuyo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 28 Koma ngati kutuwa kwa pachilondapo sikunasinthe, osafalikira pakhungu, ndipo kwayamba kuzimiririka, kumeneko ndi kutupa kwa chilonda. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera chifukwa kumeneko ndi kutukusira kwa chilonda.

29 “Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi nthenda ina yake pamutu kapena pachigama, 30 wansembe+ aziona nthendayo. Ngati pamalopo pakuoneka pozama kupitirira khungu, komanso tsitsi lachita chikasu ndipo lili patalipatali, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda yothothola tsitsi.+ Ndi khate la kumutu kapena kuchigama. 31 Koma wansembe akaona nthenda yothothola tsitsiyo, n’kuona kuti pamalopo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda, wansembe azibindikiritsa+ munthuyo masiku 7.+ 32 Wansembe azionanso nthendayo pa tsiku la 7. Ngati nthenda yothothola tsitsiyo+ sinafalikire, komanso pamalopo sipanamere tsitsi lachikasu ndipo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, 33 pamenepo munthuyo azimetedwa tsitsi lake, koma asamam’mete pamene pali nthenda yothothola tsitsipo.+ Ndipo wansembe azibindikiritsa munthuyo masiku enanso 7.

34 “Ndiyeno pa tsiku la 7 wansembe azionanso nthenda yothothola tsitsiyo. Ngati nthendayo sinafalikire pakhungu, ndipo pamalopo pakuoneka kuti si pozama kupitirira khungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Pamenepo munthuyo azichapa zovala zake ndi kukhala woyera. 35 Koma ngati nthenda yothothola tsitsiyo yafalikiradi pakhungu pambuyo pogamula kuti munthuyo ndi woyera, 36 wansembe+ azionanso munthuyo. Ngati nthenda yothothola tsitsiyo yafalikira pakhungu, wansembe asafufuzenso tsitsi lachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37 Koma ngati nthenda yothothola tsitsiyo ikuoneka kuti yasiya, ndipo pamera tsitsi lakuda, ndiye kuti nthendayo yatha. Munthuyo ndi woyera, ndipo wansembe azigamula kuti ndi woyera.+

38 “Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi zikanga+ zotuwa pakhungu lake, 39 wansembe+ aziziona. Ngati zikangazo zayamba kuzimiririka, imeneyo ndi nthenda yosaopsa imene yabuka pakhungu lake. Munthuyo ndi woyera.

40 “Mwamuna akayamba kutha tsitsi,+ limenelo ndi dazi, ndipo ndi woyera. 41 Ngati tsitsi likutha patsogolo pa mutu wake, limenelo ndi dazi la pamphumi, ndipo ndi woyera. 42 Koma ngati padazi la pankhongo kapena la pamphumi pabuka nthenda yotuwitsa khungu mofiirira, limenelo ndi khate, labuka padazi la pankhongo kapena la pamphumi. 43 Wansembe+ aziona munthuyo, ndipo ngati padazi lake la pankhongo kapena la pamphumi patuluka ziwengo zotuwa mofiirira zooneka ngati khate pakhungu lakelo, 44 ameneyo ali ndi khate ndipo ndi wodetsedwa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Ali ndi nthenda pamutu pake. 45 Ndiyeno zovala za munthu amene am’peza ndi khateyo zizing’ambidwa.+ Munthuyo asamakonze tsitsi lake+ ndipo aziphimba ndevu zake zapamlomo+ ndi kufuula kuti, ‘Wodetsedwa, wodetsedwa!’+ 46 Masiku onse pamene akudwala nthendayo azikhala wodetsedwa. Iye ndi wodetsedwa ndipo azikhala payekha. Azikhala kunja kwa msasa.+

47 “Nthenda ya khate ikabuka pachovala, kaya chovalacho ndi chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, 48 kaya yabuka cha m’litali+ kapena cha m’lifupi* mwa chovala chansalu ndi chovala chaubweya wa nkhosa, kapena pachikopa kapenanso pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa,+ 49 ndipo nthendayo ikuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pachovala kapena pachikopa, m’litali kapena m’lifupi mwa nsalu, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo iyenera kusonyezedwa kwa wansembe. 50 Pamenepo wansembe+ aziona nthendayo, ndipo azisunga chinthucho kwachokha+ masiku 7. 51 Akaona nthendayo pa tsiku la 7, n’kupeza kuti nthendayo yafalikira pachovala, m’litali kapena m’lifupi,+ kapena pachikopa, kaya amachigwiritsa ntchito yotani, nthendayo ndi khate loopsa.+ Chinthucho ndi chodetsedwa. 52 Pamenepo azitentha chovalacho, nsalu ya ubweya wa nkhosa kapena nsalu ina iliyonse,+ kapena zilizonse zopangidwa ndi chikopa, zimene zagwidwa ndi nthenda ya khateyo, chifukwa khate limenelo ndi loopsa.+ Zizitenthedwa pamoto.

53 “Koma wansembeyo akaona, n’kupeza kuti nthendayo sinafalikire pachovalacho, m’litali kapena m’lifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa,+ 54 wansembe azilamula kuti achape chinthu chogwidwa ndi nthendacho ndipo azichisungira kwachokha masiku enanso 7. 55 Wansembe aziona nthendayo, chinthucho chitachapidwa. Ngati nthendayo ikuonekabe chimodzimodzi koma sinafalikire, chinthucho ndi chodetsedwa. Muzichitentha pamoto. Chimenecho chadyedwa ndi nthendayo kuyambira mkati kapena kuyambira kunja kwake.

56 “Koma ngati wansembe waona, n’kupeza kuti nthenda ija yayamba kuzimiririka chinthucho chitachapidwa, azing’amba mbali yogwidwa ndi nthendayo pachovalacho kapena pachikopacho. 57 Koma ngati ikuonekabe pachovala, m’litali kapena m’lifupi,+ kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nthendayo ikufalikira. Chilichonse chimene chagwidwa ndi nthendayi muzichitentha+ pamoto. 58 Koma ngati nthendayo yazimiririka mutachapa chovala kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, muzichichapanso kachiwiri, pamenepo chizikhala choyera.

59 “Limeneli ndilo lamulo lokhudza nthenda ya khate yopezeka pachovala chaubweya wa nkhosa kapena chansalu,+ m’litali kapena m’lifupi, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti wansembe adziwe chinthu choyenera kugamula kuti n’choyera kapena n’chodetsedwa.”

14 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Ili likhale lamulo lokhudza wakhate+ pa tsiku limene adzam’bweretsa kwa wansembe kudzagamulidwa kuti ndi woyera.+ 3 Wansembe azipita kunja kwa msasa kukamuona. Ngati munthuyo wachira khate lake,+ 4 wansembe azim’lamula kuti atenge zofunika pa kudziyeretsa kwake. Azitenga mbalame zamoyo ziwiri zosadetsedwa,+ nthambi ya mtengo wa mkungudza,+ ulusi wofiira kwambiri+ ndi kamtengo ka hisope.+ 5 Ndipo wansembe azilamula kuti mbalame imodzi aiphere pamwamba pa madzi otunga kumtsinje,+ amene ali m’chiwiya chadothi. 6 Koma azitenga mbalame inayo pamodzi ndi nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope, n’kuziviika pamodzi ndi mbalame yamoyo ija m’magazi a mbalame imene aiphera pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija. 7 Kenako wansembe azidontheza+ magaziwo maulendo 7+ pamunthu amene akudziyeretsa ku khateyo, ndipo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Akatero, aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo.+

8 “Ndiyeno wodziyeretsayo azichapa zovala zake+ ndi kumeta tsitsi lake lonse, kenako azisamba+ ndipo azikhala woyera. Akatero, angathe kulowa mumsasa, koma azikhala kunja kwa hema wake masiku 7.+ 9 Pa tsiku la 7 azimeta tsitsi lake lonse lakumutu,+ ndevu zake zonse ndi nsidze zonse. Azimeta tsitsi lake lonse, ndipo azichapa zovala zake ndi kusamba madzi otunga kumtsinje. Akatero, azikhala woyera.

10 “Tsopano pa tsiku la 8,+ iye azitenga nkhosa zazing’ono zamphongo ziwiri zopanda chilema, ndi nkhosa yaing’ono yaikazi + imodzi yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi. Azitenganso ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake ya mbewu+ yothira mafuta, ndi muyezo umodzi* wa mafuta.+ 11 Pamenepo wansembe amene wagamula kuti munthuyo ndi woyera, azikaonetsa amene akudziyeretsayo, ndi zinthu zakezo kwa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 12 Kenako wansembeyo azitenga nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi ndi kuipereka monga nsembe ya kupalamula+ pamodzi ndi muyezo umodzi+ wa mafuta uja. Zimenezi aziziweyulira* uku ndi uku monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova. 13 Ndipo azipha nkhosa yaing’ono yamphongoyo pamalo+ amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza, pamalo oyera.+ Azichita zimenezi chifukwa nsembe ya kupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe ya kupalamula ndi yopatulika koposa.

14 “Pamenepo wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe ya kupalamula, n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja.+ 15 Akatero, wansembeyo atengeko mafuta pamuyezo umodzi+ uja ndi kuwathira pachikhatho cha dzanja lake lamanzere. 16 Ndiyeno wansembe aziviika chala chake cha kudzanja lamanja m’mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzere, ndipo azidontheza pansi ena mwa mafutawo ndi chala chakecho maulendo 7,+ pamaso pa Yehova. 17 Koma mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja pamene anam’paka magazi a nsembe ya kupalamula.+ 18 Ndiyeno mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, ndipo wansembe azim’phimbira machimo+ ake pamaso pa Yehova.

19 “Pamenepo wansembe azipereka nsembe yamachimo+ ndi kuphimba machimo a munthu amene akudziyeretsa ku chodetsa chakeyo. Kenako wansembe azipha nyama ya nsembe yopsereza. 20 Ndiyeno wansembe azipereka nsembe yopsereza ndi nsembe yambewu+ paguwa lansembe. Akatero, wansembe+ azim’phimbira machimo,+ ndipo munthuyo azikhala woyera.+

21 “Koma ngati munthuyo ali wosauka+ ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi,+ azibweretsa nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi monga nsembe ya kupalamula. Nsembeyo aziiweyulira uku ndi uku kuti am’phimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu. 22 Komanso azibweretsa ana awiri a njiwa+ kapena ana awiri a nkhunda, malinga ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 23 Ndipo azibweretsa zimenezi kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako+ pamaso pa Yehova. Azibweretsa zinthuzi pa tsiku la 8+ kuti wansembe agamule kuti munthuyo ndi woyera.+

24 “Kenako wansembe azitenga nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe ya kupalamula,+ ndi muyezo umodzi wa mafuta uja, ndipo wansembeyo aziweyulira zinthu zimenezi uku ndi uku, monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ 25 Ndiyeno wansembe azipha nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe ya kupalamula. Akatero azitenga ena mwa magazi a nsembe ya kupalamulayo n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja.+ 26 Pamenepo wansembeyo azithira ena mwa mafutawo pachikhatho cha dzanja lake lamanzere.+ 27 Akatero azidontheza+ ndi chala chake cha dzanja lamanja ena mwa mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzerewo maulendo 7, pamaso pa Yehova. 28 Kenako wansembe azipaka ena mwa mafuta amene ali pachikhatho chake m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja pamene anam’paka magazi a nsembe ya kupalamula.+ 29 Ndiyeno mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu+ pa munthu amene akudziyeretsayo, kuti am’phimbire machimo ake pamaso pa Yehova.

30 “Kenako wansembe azipereka mmodzi mwa ana a njiwa kapena m’modzi mwa ana a nkhunda, malinga ndi zimene munthuyo angakwanitse.+ 31 Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo+ ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza,+ azipereka imene angakwanitse pamodzi ndi nsembe yambewu. Pamenepo wansembe aziphimba machimo+ a munthu amene akudziyeretsayo pamaso pa Yehova.

32 “Limeneli ndi lamulo lokhudza munthu amene ali ndi nthenda ya khate, amene sangakwanitse kupeza zinthu zofunika kuti amugamule kukhala woyera.”

33 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 34 “Mukakafika m’dziko la Kanani,+ limene ine ndikukupatsani kuti likhale lanu,+ ndipo ndikakaika nthenda ya khate m’nyumba iliyonse m’dziko lanulo,+ 35 mwiniwake wa nyumbayo azibwera kwa wansembe ndikumuuza kuti, ‘Pakhoma* la nyumba yanga ndaona chinachake chooneka ngati nthenda yakhate.’ 36 Pamenepo wansembe azilamula kuti atulutse katundu m’nyumbamo iye asanafike kudzaona nthendayo. Azichita zimenezi kuti wansembe asagamule kuti chilichonse m’nyumbamo n’chodetsedwa. Akatero wansembe azibwera kudzaona nyumbayo. 37 Akaona nthendayo, n’kupeza kuti ili m’makoma a nyumba, ndipo ikuoneka ngati mawanga obiriwira monkera ku chikasu kapena ofiirira, komanso mawangawo akuoneka ozama, 38 wansembe azituluka m’nyumbamo n’kukaima pakhomo, ndipo azitseka+ nyumbayo masiku 7.

39 “Pa tsiku la 7, wansembe azibweranso kudzaona nyumbayo.+ Ngati nthendayo yafalikira m’makoma ake, 40 wansembe azilamula kuti achotse+ miyala imene ili ndi nthendayo, ndi kuti akaiponye kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 41 Ndiyeno wansembe alamule kuti apale mkati mwa nyumba yonseyo, ndi kutaya dothi lomangira limene agumulalo kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 42 Akatero azitenga miyala ina ndi kumanga pamene panali miyala yakaleyo. Kenako aziwalamula kumata nyumbayo ndi dothi lina.

43 “Koma ngati nthendayo yabwerera n’kufalikiranso m’nyumbamo, atachotsa miyala ija, kupala nyumbayo ndi kuimata, 44 wansembe+ azibweranso kudzaiona. Ngati nthendayo yafalikira m’nyumbamo, limenelo ndi khate loopsa.+ Nyumbayo ndi yodetsedwa. 45 Pamenepo azilamula kuti nyumbayo aigwetse pamodzi ndi miyala yake, matabwa ake ndi dothi lake lonse lomangira, ndipo zonsezi azitengere kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa.+ 46 Koma aliyense wolowa m’nyumbayo pa masiku amene wansembe walamula kuti munthu asalowemo,+ azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 47 Ndipo aliyense amene wagona m’nyumbayo, ndi aliyense amene wadyeramo chakudya azichapa zovala zake.+

48 “Koma ngati wansembe wabwera kudzaona nyumbayo ataimata, n’kupeza kuti nthendayo sinafalikire m’nyumbayo, wansembe azigamula kuti nyumbayo ndi yoyera chifukwa nthendayo yatha.+ 49 Ndiyeno kuti achite mwambo woyeretsa nyumbayo, azitenga mbalame ziwiri,+ nthambi ya mtengo wa mkungudza,+ ulusi wofiira kwambiri+ ndi kamtengo ka hisope. 50 Ndipo wansembe azipha mbalame imodzi pamwamba pa madzi a kumtsinje,+ amene ali m’chiwiya chadothi. 51 Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope,+ ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika m’magazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo+ maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo. 52 Ndiyeno aziyeretsa nyumbayo pogwiritsa ntchito magazi a mbalame ija, madzi otunga kumtsinje, mbalame yamoyo ija, nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope ndi ulusi wofiira kwambiri. 53 Pamenepo aziulutsa mbalame ya moyo ija pabwalo, kunja kwa mzinda. Akatero aziyeretsa+ nyumbayo, ndipo izikhala yoyera.

54 “Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda iliyonse yakhate,+ nthenda yothothoka tsitsi,+ 55 khate la pachovala+ ndi la m’nyumba, 56 chotupa, nkhanambo ndi chikanga.+ 57 Lamulo limeneli laperekedwa kuti likhale malangizo+ osonyeza pamene chinthu chili chodetsedwa ndi pamene chili choyera. Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda yakhate.”+

15 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda ya kukha+ kumaliseche, nthenda yakeyo ndi yodetsedwa. 3 Ndipo adzakhala wodetsedwa ndi nthendayo ngati akukha kumaliseche, kapena ngati maliseche ake atsekeka ndi zimene zikukhazo. Zikatere azikhala wodetsedwa.

4 “‘Bedi lililonse limene munthu wakukhayo angagonepo lizikhala lodetsedwa, ndipo chilichonse chimene angakhalepo chizikhala chodetsedwa. 5 Komanso munthu wokhudza bedi lakelo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 6 Ndipo aliyense wokhala pachinthu chimene wakukhayo anakhalapo, azichapa+ zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 7 Aliyense wokhudza thupi la munthu wanthenda yakukhayo+ azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 8 Ndipo wanthenda yakukhayo akalavulira munthu woyera, munthu woyerayo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 9 Chishalo+ chilichonse chimene wanthenda yakukhayo anakhalapo chizikhala chodetsedwa. 10 Aliyense wokhudza chilichonse chimene munthuyo wakhalapo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo munthu wonyamula zinthu zimenezi azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 11 Aliyense amene munthu wanthenda yakukhayo+ wamukhudza asanasambe m’manja, azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 12 Chiwiya chadothi chimene munthu wanthenda yakukhayo wakhudza chiziswedwa,+ ndipo chikakhala chamtengo+ chizitsukidwa.

13 “‘Ndiyeno munthu akachira nthenda yake yakukhayo, pazipita masiku 7 kuti akhale woyera,+ kenako azichapa zovala zake ndi kusamba madzi otunga kumtsinje,+ ndipo iye azikhala woyera. 14 Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, ndi kupereka mbalamezo kwa wansembe. 15 Pamenepo wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza.+ Wansembe azim’phimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo.

16 “‘Mwamuna akatulutsa umuna,+ azisamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 17 Chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse chimene pagwera umunawo chizichapidwa, ndipo chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo.+

18 “‘Mkazi akagonana ndi mwamuna, onse awiri azisamba thupi lonse, ndipo azikhala odetsedwa+ kufikira madzulo.

19 “‘Ngati mkazi akukha ndipo zimene akukhazo ndi magazi,+ azikhala masiku 7 ali wodetsedwa+ chifukwa cha kusamba+ kwakeko, ndipo aliyense womukhudza azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 20 Chilichonse chimene angagonepo pamene ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake chizikhala chodetsedwa,+ ndiponso chilichonse chimene wakhalapo chizikhala chodetsedwa. 21 Aliyense wokhudza bedi lake azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 22 Aliyense wokhudza chilichonse chimene mkaziyo anakhalapo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 23 Ndipo ngati mkaziyo anakhala pabedi kapena pachinthu china, wokhudza+ chinthu chimenecho azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 24 Mwamuna akagonana ndi mkazi ameneyu, azikhala wodetsedwa chifukwa chakuti mkaziyo akusamba.+ Zikatero, mwamunayo azikhala wodetsedwa masiku 7, ndipo bedi lililonse limene angagonepo lizikhala lodetsedwa.

25 “‘Mkazi akakha magazi kwa masiku ambiri+ pamene si nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba,+ kapena akapitiriza kukha magazi nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake itatha, masiku onse pamene iye akukha magaziwo azikhala ngati mmene amakhalira pa nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba. Iye ndi wodetsedwa. 26 Bedi lililonse limene angagonepo pa tsiku lililonse mwa masiku amene akukha magaziwo, lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi ya kusamba kwake.+ Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi ya kusamba kwake. 27 Aliyense wokhudza+ zinthuzo azikhala wodetsedwa, ndipo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28 “‘Akasiya kukha magaziko, pazipita masiku 7, kenako azikhala woyera.+ 29 Ndiyeno pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda, ndi kubwera nawo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+ 30 Pamenepo wansembe azipereka mbalame imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza.+ Wansembe azim’phimbira machimo+ pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwakeko.

31 “‘Muzionetsetsa kuti ana a Isiraeli akupewa choipitsa chilichonse, kuopera kuti angafe chifukwa choipitsa chihema changa chopatulika chimene chili pakati pawo.+

32 “‘Limeneli ndi lamulo lokhudza mwamuna wanthenda yakukha kumaliseche,+ ndi mwamuna amene watulutsa umuna+ n’kudetsedwa nawo. 33 Lamulo limeneli ndi lokhudzanso mkazi wodetsedwa chifukwa cha kusamba+ kwake, ndi aliyense amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche,+ kaya mwamuna kapena mkazi ndiponso mwamuna wogonana ndi mkazi wodetsedwa.’”

16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana awiri a Aroni, amene anafa+ chifukwa choonekera pamaso pa Yehova mosavomerezeka. 2 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni m’bale wako, kuti asamalowe konse m’malo oyera+ kuseri kwa nsalu yotchinga,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, kuopera kuti angafe,+ chifukwa ine ndidzaonekera mu mtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+

3 “Polowa m’malo oyera,+ Aroni azitenga zotsatirazi: ng’ombe yaing’ono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ 4 Azivala mkanjo wopatulika wowomba,+ kabudula wansalu+ wobisa thupi lake, lamba wansalu wa pamimba,+ ndipo azikulunga kumutu kwake ndi nduwira yansalu.+ Zimenezi ndi zovala zopatulika.+ Iye azivala zimenezi atasamba thupi lonse.+

5 “Ndiyeno khamu la ana a Isiraeli+ lizim’patsa ana a mbuzi awiri, amphongo, kuti akhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo imodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+

6 “Ndiponso Aroni azitenga ng’ombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo,+ ndipo aziphimba machimo+ ake+ ndi a nyumba yake.+

7 “Kenako azitenga mbuzi ziwiri zija ndi kuziimika pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 8 Ndipo Aroni azichita maere+ pa mbuzi ziwirizo. Maere amodzi akhale a Yehova, ndipo ena akhale a Azazeli.*+ 9 Ndiyeno Aroni azitenga mbuzi imene maere+ asonyeza kuti ndi ya Yehova, ndipo izikhala nsembe yamachimo.+ 10 Koma mbuzi imene maere asonyeza kuti ndi ya Azazeli, aziiimika yamoyo pamaso pa Yehova kuti aiphimbire machimo. Akatero aziitumiza+ m’chipululu monga ya Azazeli.+

11 “Choncho Aroni azipereka ng’ombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, kuti aphimbe machimo ake ndi a nyumba yake. Akatero azipha ng’ombe ya nsembe yake yamachimoyo.+

12 “Kenako iye azitenga chofukizira+ chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri+ zokwana manja awiri+ odzaza, ndi kulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.*+ 13 Akatero, aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova,+ ndipo utsi wa zofukizazo uzikuta chivundikiro cha Likasa,+ chimene chili pa Umboni,+ kuopera kuti angafe.

14 “Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ng’ombe yamphongoyo,+ ndi kuwadontheza ndi chala chake patsogolo pa chivundikiro, chakum’mawa. Azidontheza+ magaziwo ndi chala chake maulendo 7 patsogolo pa chivundikirocho.+

15 “Kenako azipha mbuzi ya nsembe yamachimo yoperekera anthuwo,+ n’kulowa ndi magazi ake kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Kumeneko magaziwo+ azichita nawo zimene anachita ndi magazi a ng’ombe yamphongo ija. Azidontheza magaziwo patsogolo pa chivundikiro.

16 “Ndipo aziphimba machimo a malo oyera chifukwa cha zodetsa+ za ana a Isiraeli ndi kusamvera kwawo m’machimo awo onse.+ Zimenezi azichitiranso chihema chokumanako chimene chili pakati pa ana a Isiraeli, amene ndi odetsedwa.

17 “Musamapezeke munthu wina mu chihema chokumanako kuyambira pamene iye walowa m’malo oyera kukaphimba machimo kufikira atatulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake,+ a nyumba yake ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+

18 “Akatero azituluka ndi kupita kuguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova kuti akaliphimbire machimo. Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ng’ombe yamphongo ndi a mbuzi n’kuwapaka panyanga zonse za guwa lansembe.+ 19 Ena mwa magaziwo aziwadonthezera+ paguwalo ndi chala chake maulendo 7, kuti aliyeretse ku zodetsa za ana a Isiraeli ndi kulipatula.

20 “Akamaliza kuphimbira machimo+ malo oyera, chihema chokumanako ndi guwa lansembe, azibweretsanso mbuzi yamoyo ija.+ 21 Ndipo Aroni aziika manja ake onse+ pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza+ zolakwa zonse+ za ana a Isiraeli ndiponso kusamvera kwawo m’machimo awo onse.+ Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi ija+ ndi kuipereka kwa munthu amene am’sankhiratu+ kuti akaisiye kuchipululu.+ 22 Mbuziyo izinyamula zolakwa zawo zonse+ pamutu pake ndipo aziitumiza kuchipululu.+

23 “Pamenepo Aroni azilowa m’chihema chokumanako ndi kuvula zovala zake zimene anavala polowa m’malo oyera, n’kuzisiya momwemo.+ 24 Akatero azisamba thupi lonse+ m’malo oyera+ ndi kuvala zovala zake.+ Kenako azituluka kukapereka nsembe yake yopsereza+ ndi nsembe yopsereza ya anthuwo+ ndipo aziphimba machimo ake ndi a anthuwo.+ 25 Ndiyeno azitentha mafuta a nsembe yamachimo paguwa lansembe.+

26 “Munthu+ amene anapititsa mbuzi ya Azazeli uja+ azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse.+ Akatero angathe kulowa mumsasa.

27 “Koma ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo zimene magazi ake analowa nawo m’malo oyera pokaphimba machimo, azizitulutsira kunja kwa msasa ndipo azitentha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+ 28 Munthu amene watentha zimenezi azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, akatero angathe kulowa mumsasa.

29 “M’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muzidzisautsa*+ ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale.+ 30 Pakuti pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+ 31 Limeneli ndi sabata+ lanu lopumula pa zonse ndipo muzidzisautsa. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.

32 “Wansembe amene adzadzozedwa+ ndi kupatsidwa mphamvu* kuti atumikire monga wansembe,+ kulowa m’malo+ mwa bambo ake, aziphimba machimo ndipo azivala zovala za nsalu.+ Zovala zimenezo ndi zopatulika.+ 33 Iye aziphimba machimo a malo opatulika+ koposa, chihema+ chokumanako ndi guwa lansembe.+ Aziphimbanso machimo a ansembe ndi a mpingo wonse wa anthu.+ 34 Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale,+ kuti machimo onse a ana a Isiraeli aziphimbidwa kamodzi pa chaka.”+

Motero, iye anachita monga mmene Yehova analamulira Mose.

17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Uza Aroni ndi ana ake ndi ana onse a Isiraeli kuti, ‘Yehova walamula kuti:

3 “‘“Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli akapha ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi mumsasa, kapena kunja kwa msasa, 4 koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako,+ kuti aipereke monga nsembe kwa Yehova patsogolo pa chihema cha Yehova, ameneyo adzakhala ndi mlandu wa magazi. Munthu ameneyo wakhetsa magazi, ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 5 Lamulo limeneli laperekedwa kuti nsembe zimene ana a Isiraeli akuzipereka kunja,+ azibwera nazo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako kuti azipereke kwa Yehova.+ Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe zachiyanjano kwa Yehova.+ 6 Wansembe aziwaza magazi a nyamazo paguwa lansembe la Yehova+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako, ndipo azitentha mafuta+ ake kuti likhale fungo lokhazika mtima pansi loperekedwa kwa Yehova.+ 7 Chotero asamaperekenso nsembe zawo ku ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ zimene akuchita nazo chiwerewere.+ Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale, m’mibadwo yanu yonse.”’

8 “Uwauzenso kuti, ‘Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, amene wapereka nsembe yopsereza+ kapena nsembe iliyonse, 9 koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako kuti aipereke kwa Yehova,+ munthu ameneyo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+

10 “‘Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, akadya magazi alionse,+ ndidzam’kana*+ ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. 11 Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi+ ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo.+ Zili choncho popeza magazi+ ndiwo amaphimba machimo,+ chifukwa moyo uli m’magaziwo. 12 N’chifukwa chake ndauza ana a Isiraeli kuti: “Pasapezeke munthu wodya magazi ndipo pasapezeke mlendo wokhala pakati panu+ wodya magazi.”+

13 “‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithira magazi ake pansi+ ndi kuwafotsera ndi dothi.+ 14 Pakuti moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake, chifukwa m’magazimo ndi mmene muli moyo. N’chifukwa chake ndauza ana a Isiraeli kuti: “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake.+ Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.”+ 15 Munthu aliyense amene wadya nyama imene waipeza yakufa, kapena yophedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ Kenako azikhala woyera. 16 Koma ngati sanachape zovala zakezo komanso sanasambe thupi lonse, ameneyo ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chake.’”+

18 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 3 Musachite+ zimene amachita anthu a ku Iguputo kumene munali kukhala, ndipo musakachite+ zimene amachita m’dziko la Kanani, kumene ndikukulowetsani. Musakatsatire mfundo zawo. 4 Muzisunga zigamulo zanga+ ndi kutsatira+ mfundo zanga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5 Muzisunga mfundo zanga ndi zigamulo zanga, zimene ngati munthu azitsatira adzakhaladi ndi moyo chifukwa cha mfundo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova.+

6 “‘Mwamuna aliyense pakati panu asayandikire wachibale wake aliyense kuti am’vule.*+ Ine ndine Yehova. 7 Usavule bambo ako+ ndi mayi ako. Amenewo ndi mayi ako. Usawavule.

8 “‘Usavule mkazi wa bambo ako,+ chifukwa kumeneko n’kuvula bambo ako.

9 “‘Usavule mlongo wako, mwana wamkazi wa bambo ako kapena mwana wamkazi wa mayi ako, kaya wobadwa naye m’banja limodzi kapena wobadwira m’banja lina, usawavule.+

10 “‘Usavule mwana wamkazi wa mwana wako wamwamuna ndipo usavule mwana wamkazi wa mwana wako wamkazi. Usawavule chifukwa kumeneko n’kudzichititsa manyazi.

11 “‘Usavule mwana wamkazi wa mkazi wa bambo ako, mwana wa bambo ako, chifukwa ameneyo ndi mlongo wako.

12 “‘Usavule mlongo wa bambo ako. Ameneyo ndi wachibale wa bambo ako.+

13 “‘Usavule m’bale* wa mayi ako, chifukwa ndi wachibale wa mayi ako.

14 “‘Usachitire chipongwe m’bale wa bambo ako mwa kuyandikira mkazi wake kuti um’vule, chifukwa amenewo ndi mayi ako.+

15 “‘Usavule mpongozi wako wamkazi,+ chifukwa ndi mkazi wa mwana wako. Usam’vule.

16 “‘Usavule mkazi wa m’bale wako,+ chifukwa kumeneko n’kuvula m’bale wako.

17 “‘Ukakwatira mkazi, usavule mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo kuti um’vule. Usatengenso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti um’vule. Limeneli ndi khalidwe lotayirira+ chifukwa amenewa ndi achibale.

18 “‘Ukakwatira mkazi usakwatirenso m’bale wake kuti akhale mkazi wako wachiwiri+ ndi kum’vula. Usachite zimenezi pamene mkazi wako ali moyo.

19 “‘Usayandikire mkazi kuti um’vule+ pamene ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba+ kwake.

20 “‘Usagone ndi mkazi wa mnzako* n’kukhala wodetsedwa.+

21 “‘Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe+ kwa Moleki.*+ Usanyoze+ dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi. Ine ndine Yehova.+

22 “‘Usagone ndi mwamuna+ mmene umagonera ndi mkazi.+ N’chonyansa chimenechi.

23 “‘Usagone ndi nyama iliyonse*+ n’kukhala wodetsedwa, ndipo mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo.+ Kumeneko n’kuchita zosemphana ndi chibadwa.

24 “‘Musadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu yadzidetsa ndi zonse zimenezi.+ 25 Ndiye chifukwa chake dzikolo n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha kulakwa kwake. Pamenepo dzikolo lidzataya anthu ake kunja.+ 26 Motero inu muzisunga mfundo zanga ndi zigamulo zanga.+ Ndipo aliyense wa inu, kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu,+ musachite chilichonse cha zinthu zonyansa zimenezi. 27 Pakuti anthu amene akukhala m’dzikolo musanafikemo inuyo achita zinthu zonyansa zonsezi,+ motero dzikolo n’lodetsedwa. 28 Mukapewa kuchita zimenezi, dziko silidzakusanzani chifukwa choliipitsa mmene lidzasanzira mitundu imene ikukhalamo musanafike inu.+ 29 Aliyense wa inu akadzachita chilichonse mwa zinthu zonse zonyansazi, anthu ochita zimenezi adzaphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.+ 30 Chotero muzisunga malamulo anga kuti musamachite iliyonse mwa miyambo yonyansa imene anthu akhala akuchita inu musanafike.+ Pamenepo mudzapewa kudzidetsa ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

19 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Mukhale oyera,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.+

3 “‘Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 4 Musatembenukire kwa milungu yopanda pake,+ ndipo musadzipangire milungu yachitsulo chosungunula.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 “‘Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova,+ muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni.+ 6 Muzidya nyama yoperekedwa nsembeyo pa tsiku limene mwaipereka ndi tsiku lotsatira, koma yotsala kufikira tsiku lachitatu muziitentha pamoto.+ 7 Ngati munthu wadya nyamayo pa tsiku lachitatu, wadya nyama yonyansa.+ Mulungu sadzalandira nsembe imeneyo.+ 8 Ndipo munthu wodya nyamayo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho,+ chifukwa waipitsa chinthu chopatulika cha Yehova. Munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.

9 “‘Mukamakolola zinthu za m’munda mwanu, musamachotseretu zonse m’mphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha m’munda mwanumo.+ 10 Komanso, musamakolole mphesa zotsala+ za m’munda mwanu, ndipo musamatole mphesa zimene zamwazika m’munda mwanu. Zimenezo muzisiyira wovutika ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

11 “‘Musabe,+ musanamizane+ ndipo aliyense asachitire mnzake chinyengo.+ 12 Musamalumbire zabodza m’dzina langa+ ndi kuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. 13 Usabere mnzako mwachinyengo+ ndipo usafwambe aliyense.+ Malipiro a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikira m’mawa.+

14 “‘Usatemberere munthu wogontha, ndipo usaikire munthu wakhungu chinthu chopunthwitsa.+ Uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova.

15 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka,+ ndiponso musamakondere munthu wolemera.+ Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.

16 “‘Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumachita miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.+ Ine ndine Yehova.

17 “‘Usadane ndi m’bale wako mumtima mwako.+ Mnzako um’dzudzule ndithu+ kuti usasenze naye tchimo.

18 “‘Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako.+ Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova.

19 “‘Malamulo angawa muziwasunga: Musakweranitse ziweto zanu zosiyana. Pobzala mbewu m’munda mwanu musasakanize mitundu iwiri yosiyana.+ Ndipo musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.*+

20 “‘Mwamuna akagona ndi mtsikana wantchito wofunsiridwa ndi mwamuna wina, ndipo mkaziyo sanawomboledwe m’njira ina iliyonse kapena kupatsidwa ufulu, pazikhala chilango. Iwo asaphedwe chifukwa mkaziyo anali asanakhale mfulu. 21 Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe ya kupalamula+ pakhomo la chihema chokumanako. 22 Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Azitero popereka kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe ya kupalamula ija. Pamenepo munthuyo azikhululukidwa tchimo lakelo.+

23 “‘Mukafika m’dziko limene mukupita n’kubzala mtengo uliwonse wa zipatso, muziuona ngati wosadulidwa, ndipo zipatso zake zizikhala zodetsedwa kwa inu. Muziona mtengowo kukhala wosadulidwa kwa zaka zitatu ndipo musamadye zipatso zake. 24 Koma m’chaka chachinayi zipatso zake zonse+ zizikhala zoyera ndipo muzizipereka kwa Yehova+ pa chikondwerero chachikulu. 25 M’chaka chachisanu, muzidya zipatso zake ndipo mtengowo udzakuberekerani zipatso zochuluka.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26 “‘Musadye chilichonse limodzi ndi magazi.+

“‘Musaombeze*+ ndipo musachite zamatsenga.+

27 “‘Musamete ndevu zanu zotsikira m’masaya ndipo musadule nsonga za ndevu zanu.*+

28 “‘Musamadzicheke chifukwa cha munthu wakufa,+ ndipo musamadziteme zizindikiro. Ine ndine Yehova.

29 “‘Musaipitse mwana wanu wamkazi mwa kum’sandutsa hule,+ kuti dziko lingachite uhule ndi kudzaza makhalidwe otayirira.+

30 “‘Muzisunga masabata anga+ ndipo muziopa malo anga opatulika.+ Ine ndine Yehova.

31 “‘Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu+ ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo+ ndi kudetsedwa nawo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32 “‘Anthu aimvi uziwagwadira,+ munthu wachikulire uzim’patsa ulemu+ ndipo uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova.

33 “‘Munthu wokhala m’dziko lanu monga mlendo musam’chitire zoipa.+ 34 Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondera nokha,+ chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

35 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo.+ Musamachite chinyengo poyeza utali wa chinthu, kulemera kwa chinthu+ kapena poyeza zinthu zamadzi. 36 Muzikhala ndi masikelo olondola,+ miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.* Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo. 37 Muzisunga malangizo anga onse ndi zigamulo zanga zonse, ndipo muzizitsatira.+ Ine ndine Yehova.’”

20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki,*+ aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala. 3 Ine ndidzam’kana* munthu ameneyo, ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake,+ chifukwa wapereka mwana wake kwa Moleki kuti aipitse malo anga oyera+ ndi kuipitsa dzina langa loyera.+ 4 Koma nzikazo zikanyalanyaza mwadala munthu ameneyo mwa kusamupha+ pamene wapereka aliyense mwa ana ake kwa Moleki, 5 pamenepo ineyo ndidzam’kana munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake,+ ndipo ndidzamupha pamodzi ndi onse ogwirizana naye pochita chiwerewere+ ndi Moleki, kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.

6 “‘Munthu wotembenukira kwa olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo,+ komwe n’kuchita mosakhulupirika kwa ine,* ndidzam’kana ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+

7 “‘Choncho mudzipatule monga anthu oyera,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8 Muzisunga malamulo anga.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani monga anthu oyera.+

9 “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+

10 “‘Munthu wochita chigololo ndi mkazi wa munthu wina, wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake.+ Mwamuna ndi mkazi amene achita chigololowo aziphedwa ndithu.+ 11 Mwamuna wogona ndi mkazi wa bambo ake, wavula* bambo ake.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni. 12 Mwamuna akagona ndi mpongozi wake wamkazi, onse awiri aziphedwa ndithu.+ Iwo achita chinthu chosemphana ndi chibadwa. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.+

13 “‘Mwamuna akagona ndi mwamuna mnzake, mmene mwamuna amagonera ndi mkazi, onse awiri achita chinthu chonyansa.+ Iwo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.

14 “‘Mwamuna akakwatira mkazi n’kugonanso ndi mayi a mkaziyo, limenelo ndi khalidwe lotayirira.+ Aziphedwa ndi kutenthedwa,+ onse mwamunayo ndi akaziwo, kuti khalidwe lotayirira+ lisapitirire pakati panu.

15 “‘Mwamuna akagona ndi nyama,*+ aziphedwa ndithu ndipo muziphanso nyamayo. 16 Mkazi akadzipereka kwa nyama kuti agone nayo,+ muzipha mkaziyo ndi nyamayo. Anthu ochita zimenezi aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.

17 “‘Mwamuna akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, n’kugona naye, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Chotero onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo. Iye wavula mlongo wake ndipo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.

18 “‘Mwamuna akagona ndi mkazi amene ali pa nyengo ya kusamba, onse awiri sanalemekeze magazi ake.+ Choncho onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.

19 “‘Usavule m’bale* wa mayi ako+ ndi mlongo wa bambo ako,+ chifukwa wochita zimenezi wavula wachibale wake.+ Aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho. 20 Ndipo mwamuna wogona ndi mkazi wa m’bale wa bambo ake, wavula m’bale wa bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziyankha mlandu wa tchimo lawolo. Ayenera kufa kuti asabereke ana.+ 21 Mwamuna akakwatira mkazi wa m’bale wake, wachita chinthu chonyansa.+ Iye wavula m’bale wake. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kufa kuti asabereke ana.

22 “‘Motero inu muzisunga malangizo anga onse+ ndi zigamulo zanga zonse,+ kuti dziko limene ndikukulowetsani kuti mukhalemo lisakusanzeni.+ 23 Ndipo musatsatire mfundo za mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ 24 N’chifukwa chake ndinakuuzani+ kuti: “Inuyo mudzatenga dzikolo ndipo ine ndidzalipereka m’manja mwanu kuti likhale lanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndakupatulani kwa anthu a mitundu ina.”+ 25 Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse+ ndi nyama, mbalame kapena chilichonse choyenda padziko lapansi, chimene ine ndachipatula kuti musadye pogamula kuti ndi chodetsedwa. 26 Mukhale oyera kwa ine,+ chifukwa ine Yehova ndine woyera.+ Ine ndikukupatulani kwa anthu a mitundu ina kuti mukhale anthu anga.+

27 “‘Mwamuna kapena mkazi amene amalankhula ndi mizimu kapena amene amalosera zam’tsogolo+ aziphedwa ndithu.+ Aziphedwa mwa kuponyedwa miyala. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.’”+

21 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Uza ansembe, ana a Aroni, kuti, ‘Aliyense wa inu asadziipitse chifukwa cha munthu amene wamwalira pakati pa anthu a mtundu wake.*+ 2 Koma angathe kudzidetsa ngati womwalirayo ndi wachibale wake wapafupi, mayi ake, bambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi ndi m’bale wake weniweni. 3 Angathenso kudzidetsa ngati womwalirayo ndi mlongo wake, amene ndi namwali wosakwatiwa ndiponso ndi wachibale wake weniweni. 4 Asadziipitse chifukwa cha mkazi wa mwini pakati pa anthu amtundu wake ndi kudziipitsa. 5 Asamete mpala mitu yawo,+ asamete ndevu za m’masaya mwawo+ ndipo asadzitemeteme thupi lawo.+ 6 Azikhala oyera kwa Mulungu wawo+ ndipo asaipitse dzina la Mulungu wawo,+ chifukwa iwowa amapereka nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, mkate wa Mulungu wawo,+ choncho azikhala oyera.+ 7 Wansembe asakwatire hule+ kapena mkazi amene wataya unamwali wake. Asakwatirenso+ mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati,+ chifukwa wansembeyo ndi woyera kwa Mulungu wake. 8 Choncho muzim’patula+ chifukwa ndiye wopereka mkate wa Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu,+ chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+

9 “‘Mwana wamkazi wa wansembe akadziipitsa mwa kuchita uhule, pamenepo waipitsa bambo ake. Aziphedwa ndi kutenthedwa.+

10 “‘Ndipo mkulu wa ansembe wokhala pakati pa abale ake ansembe, wodzozedwa mafuta pamutu pake,+ ndi kupatsidwa mphamvu* kuti avale zovala zaunsembe,+ asalekerere tsitsi lake osalisamala+ ndipo asang’ambe zovala zake.+ 11 Iye asayandikire munthu wakufa+ ndipo asadziipitse bambo ndi mayi ake akamwalira. 12 Asatuluke m’malo opatulika ndipo asadetse malo opatulika a Mulungu wake,+ chifukwa pamutu pake pali chizindikiro cha kudzipereka ndi mafuta odzozera a Mulungu wake.+ Ine ndine Yehova.

13 “‘Mkulu wa ansembe akafuna kukwatira, azikwatira namwali.+ 14 Asakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati, mkazi amene wataya unamwali wake kapena hule, koma azikwatira namwali pakati pa anthu amtundu wake. 15 Asaipitse ana ake pakati pa anthu amtundu wake,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndam’patula.’”+

16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17 “Lankhula ndi Aroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana ako, ku mibadwo yawo yonse, amene ali ndi chilema+ asayandikire malo opatulika kudzapereka mkate wa Mulungu wake.+ 18 Munthu akakhala ndi chilema chilichonse, asayandikire malo opatulika. Kaya akhale wakhungu, wolumala, wamphuno yokhadzuka, wa chiwalo chimodzi chachitali kwambiri kuposa chinzake,+ 19 wovulala phazi kapena dzanja, 20 wanundu, woonda,* wa diso lamatenda, wa nkhanambo, wa zipere kapena wotswanyika mavalo.+ 21 Munthu aliyense mwa ana a Aroni wansembe, amene ali ndi chilema, asayandikire guwa lansembe kudzapereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova.+ Iye ali ndi chilema. Asayandikire guwa lansembe kudzapereka mkate wa Mulungu wake.+ 22 Iye angadye mkate wa Mulungu wake kuchokera pa zinthu zopatulika koposa+ ndi pa zinthu zopatulika.+ 23 Koma asayandikire nsalu yotchinga+ ndiponso guwa lansembe,+ chifukwa iye ali ndi chilema.+ Asaipitse malo anga opatulika,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikuwapatula kuti akhale oyera.’”+

24 Pamenepo Mose anafotokoza zimenezi kwa Aroni ndi ana ake, ndiponso kwa ana onse a Isiraeli.

22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aroni ndi ana ake kuti asayandikire zinthu zopatulika za ana a Isiraeli ndi kuipitsa dzina langa loyera.+ Asayandikire zinthu zimene azipatula kuti azipereke nsembe kwa ine.+ Ine ndine Yehova. 3 Uwauze kuti, ‘M’mibadwo yanu yonse munthu aliyense wodetsedwa mwa ana anu, amene adzayandikira zinthu zopatulika, zimene ana a Isiraeli azipatula kuti azipereke nsembe kwa Yehova,+ munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pamaso panga. Ine ndine Yehova. 4 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni amene ali ndi khate+ kapena nthenda yakukha,+ asadye zinthu zopatulika kufikira atakhala woyera.+ Zikhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wokhudza munthu amene wadetsedwa chifukwa cha munthu wakufa,+ kapena mwamuna amene watulutsa umuna,+ 5 kapenanso mwamuna amene wakhudza chilichonse mwa zamoyo zodetsedwa+ zopezeka zambiri, kapena amene wakhudza munthu wodetsedwa ndi chilichonse chimene chimadetsa munthu.+ 6 Munthu wokhudza chilichonse mwa zinthu zoterezi akhale wodetsedwa kufikira madzulo ndipo asadye chilichonse mwa zinthu zopatulika, koma asambe thupi lonse.+ 7 Dzuwa likalowa akhalenso woyera, ndipo pambuyo pake akhoza kudya zina mwa zinthu zopatulika, chifukwa ndi chakudya chake.+ 8 Iye asadye nyama iliyonse imene waipeza yakufa, kapena iliyonse yophedwa ndi zilombo, chifukwa angakhale wodetsedwa.+ Ine ndine Yehova.

9 “‘Chotero azisunga malamulo anga kuti asasenze tchimo ndi kufa,+ chifukwa chosasunga malamulowo ndi kuipitsa zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndawapatula monga anthu oyera.

10 “‘Munthu wamba* asadye chopatulika chilichonse.+ Mlendo wokhala m’nyumba ya wansembe kapena munthu waganyu, asadye chopatulika chilichonse. 11 Koma munthu amene wansembe wamugula ndi ndalama zake, nayenso angathe kudya zopatulikazo. Akapolo obadwira m’nyumba ya wansembe, nawonso angadye nawo chakudya chake.+ 12 Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi munthu amene si wa m’banja la ansembe, asadye nawo zopereka zopatulika. 13 Koma mwana wa wansembe akakhala mkazi wamasiye, kapena wosiyidwa ukwati alibe mwana aliyense, ndipo wabwerera kunyumba kwa bambo ake kumene anali ali mwana,+ angadye nawo chakudya cha bambo ake.+ Koma munthu wamba asadye nawo chakudya chimenecho.

14 “‘Munthu akadya mosadziwa chinthu chopatulika,+ azibwezera chinthucho ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake asanu.+ Azipereka chinthu chopatulikacho kwa wansembe. 15 Zili choncho kuti ansembe asaipitse zinthu zopatulika za ana a Isiraeli, zimene angapereke kwa Yehova,+ 16 ndi kuchititsa anthuwo kulandira chilango pa kulakwa kwawoko chifukwa chakuti adya zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndikuwapatula kuti akhale oyera.’”

17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18 “Uza Aroni ndi ana ake ndi ana onse a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna aliyense wa nyumba ya Isiraeli, kapena mlendo wokhala mu Isiraeli amene akupereka nsembe+ pofuna kukwaniritsa lonjezo lake lililonse,+ kapena amene akupereka nsembe yake yaufulu,+ imene akuipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza, 19 azipereka nyama yopanda chilema,+ ng’ombe yamphongo, nkhosa yamphongo kapena mbuzi, kuti Mulungu akuyanjeni.+ 20 Nyama iliyonse yachilema musaipereke nsembe,+ chifukwa Mulungu sadzakuyanjani.

21 “‘Munthu akafuna kupereka nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake+ kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, azipereka ng’ombe kapena nkhosa yopanda chilema, kuti Mulungu ailandire. Izikhala yopanda chilema chilichonse. 22 Isakhale yakhungu, yothyoka chiwalo, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo kapena zipere.+ Iliyonse yokhala ndi zimenezi musaipereke kwa Yehova ndipo musaike nsembe yotentha ndi moto+ ya nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova. 23 Ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chiwalo chimodzi chachitali kwambiri kapena chachifupi kwambiri kuposa chinzake,+ mungaipereke monga nsembe yaufulu, koma Mulungu sadzailandira mukaipereka pokwaniritsa lonjezo lanu. 24 Nyama imene mavalo+ ake anawafinya, kuwatswanya, kuwathothola kapena kuwadula, musaipereke kwa Yehova, ngakhalenso m’dziko lanu musadzapereke nsembe nyama zoterezi. 25 Ndipo iliyonse mwa nyama zonse zoterezi yochokera kwa mlendo musaipereke nsembe monga chakudya cha Mulungu wanu, chifukwa ndi yowonongeka. Ili ndi chilema,+ ndipo Mulungu sadzailandira.’”+

26 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27 “Ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, izikhala ndi mayi ake masiku 7,+ koma kuyambira tsiku la 8 kupita m’tsogolo mungaipereke kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto, ndipo Mulungu adzailandira. 28 Ng’ombe kapena nkhosa, musaiphe tsiku limodzi ndi mwana wake.+

29 “Mukafuna kupereka nsembe yoyamikira kwa Yehova+ muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni. 30 Muziidya pa tsiku lomwelo.+ Musasiyeko iliyonse kufikira m’mawa.+ Ine ndine Yehova.

31 “Muzisunga malamulo anga.+ Ine ndine Yehova. 32 Musaipitse dzina langa loyera,+ m’malomwake muzindiona kukhala wopatulika pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani kuti mukhale oyera.+ 33 Ndine amene ndakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova.”

23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza+ ndiyo misonkhano yopatulika. Izi ndi zikondwerero zanga:

3 “‘Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Limeneli ndi tsiku la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito iliyonse chifukwa limeneli ndi sabata la Yehova kulikonse kumene mungakhale.+

4 “‘Zikondwerero+ za Yehova, kapena kuti misonkhano yopatulika+ imene muyenera kulengeza pa nthawi yake yoikidwiratu+ ndi iyi: 5 M’mwezi woyamba,* pa tsiku la 14 m’mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la pasika+ wa Yehova.

6 “‘Pa tsiku la 15 m’mwezi umenewu, muzichita chikondwerero cha Yehova cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa imeneyi masiku 7.+ 7 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika+ ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa. 8 Kwa masiku 7, muzipereka kwa Yehova nsembe zotentha ndi moto. Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa.’”

9 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukalowa m’dziko limene ndikukupatsani, n’kukolola mbewu za m’dzikomo, muzibweretsa kwa wansembe mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+ 11 Ndipo wansembe aziweyulira mtolowo uku ndi uku+ pamaso pa Yehova kuti Mulungu akuyanjeni. Sabata likatha, ndiyeno tsiku lotsatira, wansembe aziweyulira mtolowo uku ndi uku. 12 Pa tsiku loweyulira mtolo wanu uku ndi uku, muzipereka mwana wa nkhosa wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, kuti akhale nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova. 13 Popereka nsembe imeneyi muziperekanso nsembe yambewu. Nsembeyo izikhala ufa wosalala wothira mafuta, muyezo wake magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, yafungo lokhazika mtima pansi. Muziperekanso vinyo wa nsembe yachakumwa, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.* 14 Musadye mkate, mbewu zokazinga kapena mbewu zatsopano kufikira tsiku limeneli,+ mpaka mutabweretsa nsembe ya Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale.

15 “‘Kuchokera pa tsiku lotsatana ndi sabata, pamene munabweretsa mtolo kuti ukhale nsembe yoweyula,* muziwerenga masabata* 7,+ ndipo akwane ndendende. 16 Kuchokera pa tsiku limene sabata la 7 lakwanira, pazidutsa masiku 50,+ ndipo muzipereka nsembe yambewu zatsopano+ kwa Yehova. 17 Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate+ wa m’nyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoweyula. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Poiphika izikhala ndi chofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+ 18 Popereka mitanda ya mkateyi muziperekanso ana a nkhosa amphongo opanda chilema okwana 7,+ aliyense wa chaka chimodzi, komanso ng’ombe imodzi yaing’ono yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo. Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe yopsereza, nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. Ziziperekedwa pamodzi ndi nsembe yambewu, ndi nsembe zachakumwa kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 19 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi+ monga nsembe yamachimo, ndi ana a nkhosa amphongo awiri, aliyense wachaka chimodzi, monga nsembe yachiyanjano.+ 20 Ndipo wansembe aziweyulira uku ndi uku+ ana a nkhosa awiriwo pamodzi ndi mitanda ya mkate ya zipatso zoyambirira kucha, monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi zizikhala zinthu zopatulika kwa Yehova ndipo zizikhala za wansembe.+ 21 Muzilengeza+ pa tsiku lomweli kuti muchite msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kulikonse kumene mungakhale m’mibadwo yanu yonse.

22 “‘Mukamakolola zinthu za m’munda m’dziko lanu, musamachotseretu zonse m’mphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha m’munda mwanumo.+ Zotsalazo muzisiyira wovutika+ ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 24 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘M’mwezi wa 7,+ pa tsiku loyamba m’mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, tsiku loliza lipenga,+ tsiku la msonkhano wopatulika.+ 25 Musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa pa tsikuli, ndipo muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova.’”

26 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27 “Tsiku la 10 m’mwezi wa 7 umenewu ndi tsiku la mwambo wophimba machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzidzisautsa*+ ndi kupereka nsembe+ yotentha ndi moto kwa Yehova. 28 Pa tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sadzisautsa pa tsiku limeneli aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 30 Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga ndi kum’chotsa pakati pa anthu amtundu wake.+ 31 Musamagwire ntchito iliyonse.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 32 Ili ndi sabata lopuma pa ntchito zanu zonse,+ ndipo muzidzisautsa+ madzulo pa tsiku la 9 m’mweziwo. Muzisunga sabata kuyambira madzulo kufikira madzulo tsiku lotsatira.”

33 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 34 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Tsiku la 15 m’mwezi wa 7 umenewu, ndi tsiku lochitira Yehova chikondwerero cha misasa kwa masiku 7.+ 35 Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito iliyonse yolemetsa. 36 Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musagwire ntchito iliyonse yolemetsa.

37 “‘Zimenezi ndizo zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza monga misonkhano yopatulika+ yoperekera nsembe zotentha ndi moto+ kwa Yehova. Imeneyi ndiyo misonkhano yoperekera nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ motsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku. 38 Muzichita zimenezi kuwonjezera pa kusunga masabata a Yehova,+ kupereka mphatso zanu,+ nsembe zanu zonse za lonjezo+ ndi nsembe zanu zonse zaufulu+ zimene muyenera kupereka kwa Yehova. 39 Pa tsiku la 15 m’mwezi wa 7, pamene mwakolola zinthu za m’munda m’dziko lanu, muzichita chikondwerero+ cha Yehova masiku 7.+ Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi tsiku lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzipumanso pa ntchito zanu zonse pa tsiku la 8.+ 40 Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi zikuluzikulu za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi ya m’chigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 41 Muzichitira Yehova chikondwerero chimenechi masiku 7 pa chaka,+ m’mwezi wa 7. Limeneli ndi lamulo m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 42 Muzikhala m’misasa masiku 7.+ Mbadwa zonse za Isiraeli zizikhala m’misasa,+ 43 kuti anthu a m’mibadwo yanu yonse azidziwa+ kuti ana a Isiraeli ndinawakhalitsa m’misasa powatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

44 Pamenepo Mose anafotokozera ana a Isiraeli za zikondwerero+ za Yehova.

24 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lamula ana a Isiraeli kuti akupezere mafuta ounikira+ oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale iziyaka nthawi zonse.+ 3 Aroni azikhazika nyale pamalo ake, kunja kwa nsalu yotchinga ya Umboni m’chihema chokumanako. Nyaleyo iziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale m’mibadwo yanu yonse. 4 Nyalezo+ azikhazike pachoikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, ndipo zizikhala pamaso pa Yehova nthawi zonse.+

5 “Ndiyeno utenge ufa wosalala ndi kuphika mikate 12 yozungulira yoboola pakati. Mkate uliwonse uzipangidwa ndi ufa wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 6 Ndipo usanjikize mikateyo m’magulu awiri. Gulu lililonse likhale ndi mikate 6.+ Uike mikateyo patebulo lagolide woyenga bwino pamaso pa Yehova.+ 7 Pagulu lililonse la mikateyo uike lubani weniweni. Lubaniyo aziperekedwa nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova monga chikumbutso+ choimira mkate. 8 Sabata lililonse azikhazika mkatewo pamaso pa Yehova, ndipo uzikhala pamenepo nthawi zonse.+ Limeneli ndi pangano pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale. 9 Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera m’malo oyera,+ chifukwa wapatsidwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.”

10 Ndiyeno panali mnyamata wina amene mayi wake anali Mwisiraeli, koma bambo wake anali Mwiguputo.+ Mnyamatayu analowa pakati pa ana a Isiraeli ndipo anayamba kulimbana ndi Mwisiraeli+ wina mumsasa. 11 Kenako mnyamatayo anayamba kunyoza ndi kutukwana+ dzina la Mulungu.+ Chotero anabwera naye kwa Mose.+ Dzina la mayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. 12 Ndiyeno anam’tsekera+ kudikira kuti Yehova awauze zochita naye.+

13 Pamenepo Yehova analankhula ndi Mose kuti: 14 “Munthu wotemberera dzina la Mulungu uja, mum’tulutsire kunja kwa msasa.+ Onse amene anamumva aike manja awo+ pamutu pake ndipo khamu lonse lim’ponye miyala.+ 15 Ndiyeno uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense wotemberera Mulungu wake, aziyankha mlandu wa tchimo lake. 16 Wonyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Khamu lonse lizim’ponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo.+

17 “‘Munthu aliyense amene wakantha ndi kupheratu mnzake, nayenso aziphedwa ndithu.+ 18 Munthu amene wakantha ndi kupha chiweto cha mnzake, azibweza chiweto china, chiweto kulipira chiweto.+ 19 Munthu akapundula mnzake, zimene wachitira mnzakezo iyenso muzim’chitira zomwezo.+ 20 Kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Mmene wapundulira mnzake nayenso muzim’pundula chimodzimodzi.+ 21 Wokantha ndi kupheratu chiweto cha mnzake+ azilipira,+ koma wokantha ndi kupha munthu nayenso aziphedwa.+

22 “‘Chigamulo chilichonse chigwire ntchito mofanana pakati panu, kwa mlendo wokhala pakati panu ndi kwa nzika,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+

23 Kenako Mose anafotokoza zimenezi kwa ana a Isiraeli, ndipo iwo anatulutsa munthu wotemberera uja kunja kwa msasa ndi kum’ponya miyala.+ Motero ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.

25 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose paphiri la Sinai kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukakalowa m’dziko limene ndikukupatsani,+ muzikapumitsa dzikolo ndi kulisungitsa sabata la Yehova.+ 3 Kwa zaka 6 muzilima minda yanu, ndipo m’zaka 6 zomwezo muzidulira mitengo yanu ya mpesa ndi kukolola mbewu zanu.+ 4 Koma m’chaka cha 7 dzikolo lizisunga sabata lopuma pa zonse,+ sabata la Yehova. Musalime minda yanu, ndipo musatengulire mitengo yanu ya mpesa. 5 Musakolole mbewu zomera zokha zochokera pa zimene munakolola chaka chapita, ndipo musakololenso mphesa za m’mitengo yanu yosadulirayo. M’chaka chimenecho dziko lizipumula pa zonse. 6 Ndipo inuyo, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, waganyu wanu, mlendo wokhaliratu amene akukhala pakati panu, ndi alendo ena okhala m’nyumba mwanu, muzidya zimene zamera m’chaka cha sabatacho. 7 Zimene zamerazo zikhalenso chakudya cha ziweto zanu ndi zilombo zakutchire. Mbewu zonse zomera zokha zikhale chakudya.

8 “‘Muziwerenga masabata 7 azaka, zaka 7 kuchulukitsa maulendo 7. Masiku onse a masabata 7 azaka azikwana zaka 49. 9 Ndipo m’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muziliza lipenga la nyanga ya nkhosa lolira mokwera kwambiri.+ Muziliza lipenga la nyanga ya nkhosalo m’dziko lanu lonse pa tsiku lochita mwambo wophimba machimo.+ 10 Chaka cha 50 chizikhala chopatulika, ndipo muzilengeza ufulu* kwa anthu onse okhala m’dzikolo.+ Chizikhala Chaka cha Ufulu+ kwa inu, ndipo aliyense wa inu azibwerera kumalo ake ndi kubanja lake.+ 11 Chaka cha 50 ndi Chaka cha Ufulu kwa inu.+ Musalime minda yanu kapena kukolola mbewu zomera zokha, kapenanso kukolola mphesa za m’mitengo yosadulirayo.+ 12 Chimenecho ndi Chaka cha Ufulu. Chizikhala chopatulika kwa inu. Mutha kudya zimene zamera m’minda yanu.+

13 “‘M’Chaka cha Ufulu chimenechi, aliyense wa inu azibwerera kumalo ake.+ 14 Ukamagulitsa malonda kwa mnzako kapena kugula zinthu kwa mnzako, musamachitirane chinyengo.+ 15 Ukamagula malo kwa mnzako, uziwerenga zaka zimene zapitapo kuchokera m’Chaka cha Ufulu. Azikugulitsa malowo mogwirizana ndi zaka zimene udzakhala ukukololapo.+ 16 Ngati zaka zimene udzakhala ukukololapo n’zambiri, azikugulitsa pa mtengo wokwera,+ koma ngati zakazo zili zochepa azitsitsa mtengo wa malowo, chifukwa akukugulitsa mbewu zimene udzakhala ukukololapo. 17 Musamachitirane chinyengo,+ ndipo muziopa Mulungu wanu,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 18 Muzisunga malangizo anga ndi zigamulo zanga. Mukatero mudzakhala otetezeka m’dzikolo.+ 19 Dzikolo lidzakupatsani zipatso zake.+ Mudzadya ndi kukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mmenemo.+

20 “‘Mwina munganene kuti: “Popeza sitidzalima minda yathu ndi kukolola mbewu zathu, tidzadya chiyani m’chaka cha 7?”+ 21 Dziwani kuti ndidzakudalitsani m’chaka cha 6, ndipo dzikolo lidzakupatsani chakudya cha zaka zitatu.+ 22 Mudzalima minda yanu m’chaka cha 8, ndipo mudzakhala mukudyabe chakudya chimene munakolola chija kufikira m’chaka cha 9. Mudzadya chakalecho kufikira mutakololanso china.

23 “‘Choncho musamagulitsiretu malo anu mpaka kalekale+ chifukwa dzikolo ndi langa.+ Kwa ine, inu ndinu alendo m’dziko langa.+ 24 Ndipo m’dziko lanu lonselo, munthu azikhala ndi ufulu wogulanso malo ake.+

25 “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+ 26 Munthu akakhala wopanda womuwombola, koma wapanga phindu lalikulu ndipo wapeza ndalama moti atha kuwombola malo ake, 27 aziwerenga zaka zimene zapitapo kuchokera pamene anagulitsa malowo, ndipo azibweza ndalama zotsala kwa munthu amene anagula malowo. Akatero azibwerera kumalo akewo.+

28 “‘Koma ngati munthu wogulitsa malo sanapeze ndalama zoti angabwezere kwa wogulayo, malo amene anagulitsawo apitirizebe kukhala a munthu amene anawagulayo kufikira Chaka cha Ufulu.+ M’chaka chimenecho malowo azibwezedwa kwa mwiniwake ndipo wogulitsa maloyo azibwerera kumalo akewo.+

29 “‘Munthu akagulitsa nyumba mumzinda wokhala ndi linga, azikhala ndi ufulu woiwombola chaka chimodzi chisanathe kuchokera pamene anaigulitsa. Azikhala ndi ufulu umenewu+ kwa chaka chathunthu. 30 Koma ngati sanaiwombole chaka chimodzicho chisanathe, nyumba imene ili mumzinda wokhala ndi linga izikhala ya wogulayo mpaka kalekale, m’mibadwo yake yonse, ndipo isabwezedwe m’Chaka cha Ufulu. 31 Koma nyumba zimene zili m’midzi yopanda linga zizitengedwa monga mbali ya munda wa kunja kwa mzinda. Ufulu woiwombola+ uzikhalapobe, ndipo m’Chaka cha Ufulu+ izibwezedwa kwa mwiniwake.

32 “‘M’mizinda ya Alevi, Aleviwo azikhala ndi ufulu wowombola nyumba zawo za m’mizindamo mpaka kalekale.+ 33 Ndipo ngati Mlevi anagulitsa nyumba mumzinda wawo ndipo sanaiwombole, izibwezedwa kwa Mleviyo m’Chaka cha Ufulu.+ Zizikhala choncho chifukwa nyumba za m’mizinda ya Alevi pakati pa ana a Isiraeli ndi za Aleviwo basi.+ 34 Komanso, asagulitse malo odyetserako ziweto+ ozungulira mizinda yawo, chifukwa amenewo ndi malo awo mpaka kalekale.

35 “‘M’bale wanu akasauka pakati panu+ ndipo sangathe kudzisamala, muzim’thandiza.+ Iye ayenera kukhala ndi moyo mmene mlendo wokhala pakati panu+ alili ndi moyo. 36 Musamalandire chiwongoladzanja kwa iye kapena kumukongoza mwa katapira,*+ koma muziopa Mulungu wanu.+ Mnansi wanu ayenera kukhala ndi moyo pakati panu. 37 Musam’kongoze ndalama kuti adzabweze chiwongoladzanja,+ ndipo musakongoze chakudya chanu mwa kuchititsa katapira. 38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo, kuti ndikupatseni dziko la Kanani.+ Ndinachita izi kuti ndikusonyezeni kuti ine ndine Mulungu wanu.+

39 “‘M’bale wanu akasauka pakati panu n’kudzigulitsa kwa inu,+ musam’gwiritse ntchito ngati kapolo.+ 40 Mum’tenge ngati waganyu,+ ndiponso ngati mlendo. Akutumikireni kufikira Chaka cha Ufulu. 41 M’chaka chimenecho iye ndi ana ake amasuke ndi kubwerera kwa achibale ake. Abwerere kumalo a makolo ake.+ 42 Pakuti ana a Isiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Asamadzigulitse mmene amadzigulitsira akapolo. 43 Musamupondereze ndi kumuchitira nkhanza,+ ndipo muziopa Mulungu wanu.+ 44 Kapolo wanu wamwamuna ndi kapolo wanu wamkazi azichokera ku mitundu yokuzungulirani. Muzigula kapolo wamwamuna kapena wamkazi kuchokera ku mitundu imeneyi. 45 Muzigulanso akapolo kuchokera kwa ana a alendo okhala pakati panu,+ ndi ku mabanja okhala pakati panu, amene ana a alendowo anaberekera m’dziko lanu. Muzigula amenewa kuti akhale akapolo anu. 46 Ndipo akapolowa muzisiyira ana anu monga cholowa chawo mpaka kalekale.+ Amenewa ndiwo azikhala akapolo* anu, koma abale anu, ana a Isiraeli, musawapondereze ndi kuwachitira nkhanza.+

47 “‘Mlendo wokhala pakati panu akalemera, ndipo m’bale wanu amene akukhala naye pafupi wasauka, moti wakadzigulitsa kwa mlendoyo, kapena kwa wina wa m’banja la mlendoyo, 48 m’bale wanuyo azikhalabe ndi ufulu wowomboledwa.+ Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola.+ 49 Komanso m’bale wa bambo ake, mwana wa m’bale wa bambo akewo, wachibale wake aliyense wapafupi,+ kapena kuti aliyense wa m’banja lake angathe kumuwombola.

“‘Kapenanso mwiniwakeyo akalemera, azidziwombola.+ 50 Iye aziwerengera wom’gulayo zaka zotsala kuchokera pamene anadzigulitsa kukafika Chaka cha Ufulu,+ ndipo ndalama zimene anam’gulira zizigwirizana ndi kuchuluka kwa zaka.+ Azim’gwirira ntchito mofanana ndi waganyu.+ 51 Ngati kwatsala zaka zochuluka, ndalama zake zodziwombolera zizigwirizana ndi zaka zimene zatsala, kuchotsera pa ndalama zimene anam’gulira. 52 Koma ngati kwatsala zaka zochepa kuti Chaka cha Ufulu chifike,+ aziwerenga zaka zotsalazo, ndipo azipereka ndalama zodziwombolera zogwirizana ndi zaka zotsalazo. 53 Azim’gwirira ntchito mofanana ndi waganyu+ chaka ndi chaka. Asamamupondereze ndi kumuchitira nkhanza+ pamaso panu. 54 Koma ngati sangathe kudziwombola mwa njira imeneyi, azimasuka m’Chaka cha Ufulu,+ iye pamodzi ndi ana ake.

55 “‘Pakuti kwa ine ana a Isiraeli ndi akapolo. Ndi akapolo anga+ amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+

26 “‘Musadzipangire milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika. Musaike mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mochita kugoba+ m’dziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 2 Muzisunga masabata anga+ ndi kuopa malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.

3 “‘Mukapitiriza kutsatira malangizo anga ndi kusunga malamulo anga,+ 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.+ 5 Pamenepo, mudzakhala mukupuntha zimene mwakolola kufikira nyengo yokolola mphesa, ndipo mudzakhala mukukolola mphesa kufikira nyengo yofesa mbewu. Mudzadya mkate wanu ndi kukhuta,+ ndipo mudzakhala otetezeka m’dziko lanu.+ 6 Ndidzakupatsani mtendere m’dzikolo,+ moti mudzagona pansi popanda wokuopsani.+ M’dziko lanu simudzapezeka zilombo zoopsa zakutchire,+ ndipo simudzadutsa lupanga.+ 7 Mudzathamangitsa adani anu+ ndi kuwagonjetsa ndi lupanga. 8 Anthu asanu mwa inu adzathamangitsa adani 100, ndipo anthu 100 adzathamangitsa adani 10,000, moti mudzagonjetsa adani anu ndi lupanga.+

9 “‘Pamenepo ndidzakucheukirani,+ kukuchititsani kubereka ana ambiri ndi kukuchulukitsani.+ Ndipo ndidzasunga pangano langa ndi inu.+ 10 Mudzadya chakudya cha chaka chapita,+ ndipo chimenecho mudzachitulutsa kuti mupeze malo oikapo chatsopano. 11 Ine ndidzaika chihema changa chopatulika pakati panu,+ ndipo sindidzanyansidwa nanu.+ 12 Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu,+ ndipo inu mudzakhala anthu anga.+ 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti musakhale akapolo a Aiguputo.+ Ndinathyola goli lanu ndi kukuchititsani kuyenda mowongoka.+

14 “‘Koma ngati simudzandimvera kapena kutsatira malamulo onsewa,+ 15 ndipo mukadzakana malangizo anga,+ n’kunyansidwa ndi zigamulo zanga, moti mwakana kutsatira malamulo anga onse, n’kufika pophwanya pangano langa,+ 16 pamenepo ine ndidzakuchitani zotsatirazi: pokulangani ndidzakugwetserani zoopsa za chifuwa chachikulu+ ndi kuphwanya kwa thupi koopsa, kumene kudzachititsa maso anu khungu+ ndi kukufooketsani.+ Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+ 17 Ine ndidzakukanani,* ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+

18 “‘Koma ngati simudzandimverabe pambuyo poona zinthu zimenezi, pamenepo ndidzakulangani mowirikiza ka 7 kuposa poyamba chifukwa cha machimo anu.+ 19 Ndidzathyola kunyada kwanuko, ndi kuchititsa kumwamba kukhala ngati chitsulo+ ndi nthaka yanu ngati mkuwa. 20 Motero mphamvu zanu zidzathera pachabe, chifukwa nthaka yanu siidzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda mwanu siidzakupatsani zipatso zake.+

21 “‘Koma mukapitirizabe kuchita zosemphana ndi zofuna zanga, osafuna kundimvera, pamenepo ndidzakukanthani mowirikiza ka 7 malinga ndi machimo anu.+ 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu, ndi kuchepetsa chiwerengero chanu, moti m’misewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+

23 “‘Ngati simudzalola kuti ndikukonzeni ndi zinthu zimenezi,+ ndipo mukupitiriza kuyenda motsutsana nane, 24 pamenepo, ineyo ndidzatsutsana nanu,+ ndipo ndidzakukanthani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu.+ 25 Ndidzabweretsa lupanga pa inu lobwezera chilango+ chifukwa cha pangano.+ Pamenepo mudzathawira m’mizinda yanu, ndipo ndidzakutumizirani mliri pakati panu+ ndi kukuperekani m’manja mwa mdani.+ 26 Ndikadzathyola ndodo zanu zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani mochita kukuyezerani pamuyezo.+ Chotero mudzadya koma simudzakhuta.+

27 “‘Koma ngati simudzandimvera zinthu zimenezi zitakuchitikirani, n’kupitirizabe kuyenda motsutsana nane,+ 28 pamenepo ndidzatsutsana nanu koopsa,+ ndipo ineyo ndidzakukwapulani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu.+ 29 Chotero mudzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ 30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+ 31 Mizinda yanu ndidzaiwononga ndi lupanga+ ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu,+ komanso sindidzalandira nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi.+ 32 Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja,+ ndipo adani anu amene adzakhala m’dzikolo adzaliyang’anitsitsa modabwa.+ 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.

34 “‘Pa masiku onse amene dzikolo lidzakhala bwinja, lidzabweza masabata ake, inu muli m’dziko la adani anu. Nthawi imeneyo, dziko lidzasunga sabata ndipo lidzabweza masabata ake.+ 35 Masiku onse amene dzikolo lidzakhala bwinja lidzakhala likusunga sabata, chifukwa silinasunge sabata, pakuti inuyo simunasunge masabata anu pamene munali kukhala m’dzikolo.

36 “‘Ndidzaika mantha m’mitima ya otsala pakati panu+ amene ali m’dziko la adani awo, moti adzathawa m’tswatswa wa tsamba louluka, ndipo adzathawa ngati kuti akuthawa lupanga. Pamenepo adzagwa popanda munthu wowathamangitsa.+ 37 Iwo adzagwetsana okhaokha ngati kuti akuthawa lupanga, koma popanda munthu wowathamangitsa. Simudzatha n’komwe kulimbana ndi adani anu.+ 38 Mudzatheratu pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo dziko la adani anu lidzakumezani. 39 Otsala pakati panu, adzazunzika+ chifukwa cha zolakwa zawo m’mayiko a adani awo. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ mmene makolowo anazunzikira. 40 Chotero adzavomereza kuti iwo komanso makolo awo anayenda motsutsana nane,+ anandichimwira+ ndi kundichitira mosakhulupirika. 41 Zimenezi zinachititsa kuti ine nditsutsane nawo+ ndi kuwatengera kudziko la adani awo.+

“‘Izi zinachitika kuti mwina mitima yawo yosadulidwayo+ ingadzichepetse,+ ndi kulipira chifukwa cha zolakwa zawo. 42 Chotero ndidzakumbukira pangano langa limene ndinachita ndi Yakobo.+ Ndidzakumbukiranso pangano langa ndi Isaki+ komanso ndi Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pa nthawiyo, adzakhala atasiya dziko lawo, ndipo dzikolo lidzakhala likubweza masabata ake+ pamene lidzakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo adzakhala akulipira chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa chakuti anakana zigamulo zanga+ ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+ 44 Koma ngakhale kuti padzachitika zonsezi, pamene iwo akukhala m’dziko la adani awo, sindidzawakana+ kapena kunyansidwa nawo+ moti n’kuwafafaniziratu, kuphwanya pangano langa+ ndi iwo, chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Ndipo ndidzakumbukira m’malo mwawo pangano limene ndinachita ndi makolo awo,+ amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo, anthu a mitundu ina akuona.+ Ndidzachita zimenezi kuti ndiwasonyeze kuti ndine Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”

46 Amenewa ndiwo malangizo, zigamulo+ ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa iye ndi ana a Isiraeli m’phiri la Sinai, kudzera mwa Mose.+

27 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu akapanga lonjezo lapadera+ lopereka munthu mnzake kwa Yehova pa mtengo woikidwiratu, 3 ngati munthu woperekedwayo ndi wamwamuna, wazaka zapakati pa 20 ndi 60, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli asiliva 50, pamuyezo wolingana ndi sekeli la kumalo oyera.* 4 Koma ngati munthuyo ndi wamkazi, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 30. 5 Ndipo ngati munthu woperekedwayo ndi wazaka zapakati pa 5 ndi 20, akakhala wamwamuna mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 20, koma akakhala wamkazi mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 10. 6 Ngati msinkhu wa munthuyo ndi wapakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, akakhala wamwamuna mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli asiliva asanu,+ ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli asiliva atatu.

7 “‘Ndiyeno ngati zaka za munthu woperekedwayo ndi zoyambira pa 60 kupita m’tsogolo, akakhala wamwamuna, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 15, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli 10. 8 Koma ngati wolonjezayo ndi wosauka moti sangakwanitse mtengo woikidwiratuwo,+ azikaonetsa munthu woperekedwayo kwa wansembe, ndipo wansembe azinena mtengo wa munthuyo.+ Wansembe adzanena mtengo umene wolonjezayo angakwanitse.+

9 “‘Koma ngati chopereka chake ndi nyama yonga imene anthu amapereka nsembe kwa Yehova, iliyonseyo imene angapereke kwa Yehova izikhala yopatulika.+ 10 Asaichotse ndi kuikapo ina, ndipo asasinthanitse yabwino ndi yoipa kapena yoipa ndi yabwino. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndiponso imene waisinthanitsa nayo, zizikhala zopatulika. 11 Koma ngati chopereka chake ndi nyama yodetsedwa+ imene anthu sangaipereke nsembe kwa Yehova,+ azikaonetsa nyamayo kwa wansembe.+ 12 Ndipo wansembe azinena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyamayo ilili, kaya ndi yabwino kapena yoipa. Mtengo wa nyamayo+ umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 13 Koma ngati akufuna kuiwombola, azipereka mtengo woikidwiratu wa nyamayo ndi kuwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a mtengowo.

14 “‘Munthu akapereka* nyumba yake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, wansembe aziiona ndi kunena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyumbayo ilili, kaya ndi yabwino kapena ayi.+ Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 15 Koma wopereka nyumbayo akafuna kuiwombola, azipereka mtengo woikidwiratu wa nyumbayo ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ Akatero azitenganso nyumbayo kukhala yake.

16 “‘Ngati wapereka mbali ina ya munda wake+ kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angabzalepo. Ngati angabzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri,*+ ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50. 17 Ngati wapereka mundawo kuyambira m’Chaka cha Ufulu+ kupita m’tsogolo, mtengo wake woikidwiratu uzikhala womwewo, wogwirizana ndi mbewu. 18 Koma ngati wapereka mundawo Chaka cha Ufulu chitadutsa, wansembe azimuwerengera mtengo wake mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kukafika m’Chaka cha Ufulu chotsatira, ndipo azichotsera pa mtengo wake woikidwiratu.+ 19 Koma ngati wopereka mundayo angauwombole, azipereka mtengo wake woikidwiratu ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake asanu, akatero mundawo uzikhaladi wake.+ 20 Ngati mundawo sanauwombole ndipo wagulitsidwa kwa munthu wina, sangathenso kuuwombola. 21 Ndiyeno pamene mundawo ukubwezedwa m’Chaka cha Ufulu, uziperekedwa kwa Yehova mpaka kalekale.+ Mundawo ndi wopatulika ndipo uzikhala wa wansembe.+

22 “‘Koma ngati wapatula munda umene anachita kugula kuti ukhale wa Yehova, munda umene sunali wake weniweni,+ 23 wansembe azimuwerengera mtengo wake, malinga ndi zaka zimene zatsala kuti Chaka cha Ufulu chifike, ndipo tsiku lomwelo azipereka mtengo umene wansembe wawerengerawo.+ Ndalamazo ndi zopatulika kwa Yehova.+ 24 M’Chaka cha Ufulu mundawo udzabwezedwa kwa mwiniwake weniweni amene anaugulitsa.+

25 “‘Mtengo woikidwiratu uliwonse uzikhala wolingana ndi sekeli la kumalo oyera. Sekeli limodzi lizikwana magera* 20.+

26 “‘Munthu asapatule nyama iliyonse yoyamba kubadwa kuti ikhale yoyera, chifukwa iliyonse yoyamba kubadwa ndi ya Yehova.+ Kaya ndi ng’ombe kapena nkhosa, ndi za Yehova.+ 27 Koma nyama yodetsedwa+ yoyamba kubadwa angaiwombole. Ngati munthu akufuna kuiwombola azipereka mtengo wa nyamayo n’kuwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ Koma ngati mwiniwake wa nyamayo saiwombola wansembe aziigulitsa pa mtengo woikidwiratu.

28 “‘Ngati munthu watenga munthu mnzake, nyama kapena munda wake n’kuupatula kuti ukhale woyera kwa Yehova kwamuyaya,* kapena akapereka munthuyo, nyama kapena munda kwa Mulungu kuti auwononge,+ sungagulitsidwe kapena kuwomboledwa.+ Munthu, nyama kapena munda umenewo ndi wopatulika koposa. Zimenezi ndi za Yehova. 29 Munthu aliyense woperekedwa kwa Mulungu kuti awonongedwe sangathe kuwomboledwa.+ Ameneyo aziphedwa ndithu.+

30 “‘Chakhumi* chilichonse+ cha zinthu za m’dzikolo, kaya ndi zokolola m’munda kapena zipatso za m’mitengo, ndi cha Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova. 31 Ndipo munthu akafuna kuwombola chakhumi chake, azipereka mtengo wa chakhumicho n’kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ 32 Ng’ombe kapena nkhosa iliyonse ya 10, pa nyama zonse zodutsa pansi pa ndodo,*+ iliyonse ya 10 iziperekedwa kwa Yehova ndipo izikhala yopatulika. 33 Asaifufuze ngati ili yabwino kapena yoipa, ndiponso asaisinthanitse ndi ina. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndi imene waisinthanitsa nayo, zizikhala zopatulika.+ Sangathe kuiwombola.’”

34 Amenewa ndiwo malamulo+ amene Yehova anapatsa Mose paphiri la Sinai+ kuti apereke kwa ana a Isiraeli.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:13.

Kwenikweni, “kudula” kumeneku sikunali kuchotseratu mutu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Uchi.” Zikuoneka kuti uwu si uchi wa njuchi koma ndi madzi azipatso, chifukwa ukutchedwa zipatso zoyambirira. (Le 2:12; 2Mb 31:5)

N’kutheka kuti anali kuperekanso balere.

“Chiwindi” ena amati “mphafa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “temberero.” Popereka chilengezo chimenechi ankatchulanso temberero kwa wochimwayo kapena mboni imene ikudziwa za nkhaniyo ngati italephera kudzapereka umboni wake.

“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 30:13.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Dzombe limene likunenedwa pano ndi dzombe lokhwima lokhala ndi mapiko.

Ena amati “saka.”

Kapena kuti “nthendayo sangapatsire ena.”

Mawu ake enieni, “ulusi wowombera nsalu woyenda m’litali kapena m’lifupi.”

“Muyezo umodzi” umenewu ndi wofanana ndi gawo limodzi mwa magawo atatu a lita.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “mkati mwa nsalu yotchinga.”

“Kudzisautsa” pano kungatanthauze kusala chakudya ndiponso kudzimana zinthu zina.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.

Olambira ziwanda zooneka ngati mbuzizo anali kuganiza kuti ziwandazo zinali zolengedwa za ubweya wambiri zooneka ngati tonde wa mbuzi.

Mawu ake enieni, “ndidzaika nkhope yanga motsutsana naye.”

Apa akunena za kugonana.

Ameneyu ndi wamkazi.

Mawu ake enieni, “Usapereke umuna wako kwa mkazi wa mnzako.”

Zimenezi ziyenera kuti zinaphatikizapo kupereka ana nsembe.

Mawu ake enieni, “Usapereke umuna wako kwa nyama iliyonse.”

Kutanthauza chovala chimene nsalu yake anaiwomba mophatikiza ulusi wa thonje ndi ubweya wa nkhosa. Onani De 22:11.

Mawu akuti “kuwombeza” akutanthauza kufuna kudziwa zam’tsogolo; kapena kufufuza ngati zochitika kapena zinthu zinazake zikulosera kuti m’tsogolo mudzachitika zabwino kapena zoipa.

Apa akuwaletsa kuchita zimene anthu akunja anali kuchita, koma sakutanthauza kuti asayepule ndevu zawo ngakhale pang’ono.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa Le 18:21.

Onani mawu a m’munsi pa Le 17:10.

Mawu ake enieni, “kuchita nawo chiwerewere.”

Onani mawu a m’munsi pa Le 18:6.

Mawu ake enieni, “akapereka umuna wake kwa nyama.”

Onani mawu a m’munsi pa Le 18:13.

Wansembe akanatha kudziipitsa mwa kukhudza mtembo kapena kulira nawo maliro.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.

Apa mwina akunena za munthu wamfupi monyanyira kapena woonda chifukwa cha matenda.

Kapena kuti munthu amene si wa m’banja la Aroni.

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.

“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.

Kapena kuti “milungu.”

Onani mawu a m’munsi pa Le 16:29.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kapena kuti “kumasulidwa kwa akapolo.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.

Mawu ake enieni, “antchito.”

Onani mawu a m’munsi pa Le 17:10.

Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pamawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 30:13.

Mawu ake enieni, “akapatula.”

“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.

Onani Zakumapeto 12.

Kapena kuti “kuupereka ku chiwonongeko.”

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

M’busa anali kuwerenga ziweto zake mwa kuzidutsitsa pansi pa ndodo yake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena