Numeri
1 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose m’chipululu cha Sinai,+ m’chihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri m’chaka chachiwiri, atatuluka m’dziko la Iguputo.+ Iye anati: 2 “Uwerenge+ khamu lonse la ana a Isiraeli malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, n’kulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi. 3 Uwerenge kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ aliyense woyenerera kupita kunkhondo pakati pa Aisiraeli.+ Iweyo ndi Aroni muwalembe m’kaundula malinga ndi magulu awo a asilikali.
4 “Mukhale ndi amuna ena okuthandizani, mwamuna mmodzi pafuko lililonse. Aliyense akhale woti ndi mtsogoleri wa nyumba ya makolo ake.+ 5 Nawa mayina a amuna amene akuthandizeni: Kuchokera ku fuko la Rubeni,+ Elizuri+ mwana wa Sedeuri, 6 kuchokera ku fuko la Simiyoni,+ Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai, 7 kuchokera ku fuko la Yuda,+ Naasoni+ mwana wa Aminadabu, 8 kuchokera ku fuko la Isakara,+ Netaneli+ mwana wa Zuwara, 9 kuchokera ku fuko la Zebuloni,+ Eliyabu+ mwana wa Heloni. 10 Mwa ana a Yosefe+ kuchokera ku fuko la Efuraimu,+ Elisama mwana wa Amihudi, kuchokera ku fuko la Manase,+ Gamaliyeli mwana wa Pedazuri, 11 kuchokera ku fuko la Benjamini,+ Abidana+ mwana wa Gidoni, 12 kuchokera ku fuko la Dani,+ Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai, 13 kuchokera ku fuko la Aseri,+ Pagiyeli+ mwana wa Okirani, 14 kuchokera ku fuko la Gadi,+ Eliyasafu+ mwana wa Deyueli,+ 15 kuchokera ku fuko la Nafitali,+ Ahira+ mwana wa Enani. 16 Amenewa ndiwo osankhidwa a khamu la anthuwo, atsogoleri a mafuko+ a makolo awo. Aliyense wa iwo ndi mtsogoleri wa anthu masauzande mu Isiraeli.”+
17 Choncho Mose ndi Aroni anatengadi amuna amene anatchulidwa mayinawo. 18 Atatero, anasonkhanitsa anthu onse pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri. Anawasonkhanitsa n’cholinga chakuti awalembe m’kaundula+ kuti adziwe mibadwo yawo malinga ndi mabanja awo, ndiponso nyumba za makolo awo. Anawalemba mayina kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ mmodzi ndi mmodzi. 19 Chotero Mose anawerenga anthuwo+ m’chipululu cha Sinai, monga mmene Yehova anamulamulira.
20 Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba amuna onse kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 21 Onse olembedwa mayina a fuko la Rubeni anakwana 46,500.+
22 Mbadwa za Simiyoni,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba amuna onse kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 23 Onse olembedwa mayina a fuko la Simiyoni analipo 59,300.+
24 Mbadwa za Gadi,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 25 Onse olembedwa mayina a fuko la Gadi+ analipo 45,650.+
26 Mbadwa za Yuda,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 27 Onse olembedwa mayina a fuko la Yuda analipo 74,600.+
28 Mbadwa za Isakara,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 29 Onse olembedwa mayina a fuko la Isakara analipo 54,400.+
30 Mbadwa za Zebuloni,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 31 Onse olembedwa mayina a fuko la Zebuloni analipo 57,400.+
32 Mbadwa za Yosefe za fuko la Efuraimu+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 33 Onse olembedwa mayina a fuko la Efuraimu+ analipo 40,500.+
34 Mbadwa za Manase+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 35 Onse olembedwa mayina a fuko la Manase analipo 32,200.+
36 Mbadwa za Benjamini,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 37 Onse olembedwa mayina a fuko la Benjamini analipo 35,400.+
38 Mbadwa za Dani,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 39 Onse olembedwa mayina a fuko la Dani analipo 62,700.+
40 Mbadwa za Aseri,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 41 Onse olembedwa mayina a fuko la Aseri analipo 41,500.+
42 Mbadwa za Nafitali,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 43 Onse olembedwa mayina a fuko la Nafitali analipo 53,400.+
44 Amenewa ndi amene analembedwa mayina, amene Mose ndi Aroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri 12, amuna achiisiraeli. Aliyense wa amunawa anaimira nyumba za makolo ake. 45 Choncho ana a Isiraeli onse olembedwa mayina malinga ndi nyumba za makolo awo, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo pakati pa Aisiraeli, 46 onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+
47 Koma Alevi+ malinga ndi fuko la makolo awo sanawawerengere pamodzi ndi enawo.+ 48 Sanawawerenge chifukwa Yehova anali atauza Mose kuti: 49 “A fuko la Levi okha usawalembe mayina, ndipo usawawerengere pamodzi ndi ana a Isiraeli enawo.+ 50 Iweyo uike Aleviwo kukhala oyang’anira chihema cha Umboni+ ndi ziwiya zake zonse, ndi chilichonse cha mmenemo.+ Iwowo ndi amene azinyamula chihema chopatulikacho ndi ziwiya zake zonse.+ Ndi amenenso azitumikira+ pachihemapo, ndipo azimanga misasa yawo mochizungulira.+ 51 Pa nthawi yosamutsa chihema chopatulika, Aleviwo azichipasula,+ ndipo mukafika pomanga msasa, iwo ndiwo azimanga chihemacho. Aliyense amene si Mlevi akayandikira chihemacho aziphedwa.+
52 “Ana a Isiraeli azimanga mahema awo, aliyense malinga ndi msasa wawo, munthu aliyense malinga ndi gulu lake la mafuko atatu,+ malinga ndi magulu awo a asilikali. 53 Alevi azimanga mahema awo mozungulira chihema cha Umboni kuti mkwiyo+ wa Mulungu usawayakire ana a Isiraeli. Aleviwo azitumikira pachihema cha Umbonicho.”+
54 Ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose. Anachitadi momwemo.+
2 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti: 2 “Ana a Isiraeli azikhoma mahema awo, aliyense azikhoma hema wake m’chigawo chawo cha mafuko atatu,+ potsata chizindikiro cha nyumba ya makolo ake. Azikhoma mahema awo mozungulira chihema chokumanako komanso moyang’ana chihemacho.
3 “Chigawo cha mafuko atatu cha Yuda ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kum’mawa kotulukira dzuwa. Mtsogoleri wa ana a Yuda ndi Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 4 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 74,600.+ 5 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Isakara.+ Mtsogoleri wa ana a Isakara ndi Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 6 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 54,400.+ 7 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa ana a Zebuloni ndi Eliyabu,+ mwana wa Heloni. 8 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 57,400.+
9 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Yuda alipo 186,400. Amenewa azikhala oyamba kunyamuka.+
10 “Chigawo cha mafuko atatu cha Rubeni+ ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kum’mwera. Mtsogoleri wa ana a Rubeni ndi Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 11 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 46,500.+ 12 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Simiyoni. Mtsogoleri wa ana a Simiyoni ndi Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 13 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 59,300.+ 14 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Gadi. Mtsogoleri wa ana a Gadi ndi Eliyasafu,+ mwana wa Reueli. 15 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 45,650.+
16 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Rubeni alipo 151,450. Amenewa azikhala achiwiri kunyamuka.+
17 “Posamutsa chihema chokumanako,+ gulu la msasa wa Alevi+ lizikhala pakati pa magulu a misasa ina.
“Dongosolo limene azilitsatira posamuka,+ n’limenenso azitsatira pomanga misasa yawo, aliyense m’malo ake, malinga ndi chigawo chawo cha mafuko atatu.
18 “Chigawo cha mafuko atatu cha Efuraimu+ ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kumadzulo. Mtsogoleri wa ana a Efuraimu ndi Elisama,+ mwana wa Amihudi. 19 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 40,500.+ 20 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Manase.+ Mtsogoleri wa ana a Manase ndi Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 21 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 32,200.+ 22 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Benjamini.+ Mtsogoleri wa ana a Benjamini ndi Abidana,+ mwana wa Gidoni. 23 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 35,400.+
24 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Efuraimu alipo 108,100. Amenewa azikhala achitatu kunyamuka.+
25 “Chigawo cha mafuko atatu cha Dani ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kumpoto. Mtsogoleri wa ana a Dani ndi Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 62,700.+ 27 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Aseri. Mtsogoleri wa ana a Aseri ndi Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 28 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 41,500.+ 29 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Nafitali.+ Mtsogoleri wa ana a Nafitali ndi Ahira,+ mwana wa Enani. 30 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 53,400.+
31 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Dani alipo 157,600. Amenewa azikhala omalizira kunyamuka,+ malinga ndi zigawo za Aisiraeli za mafuko atatuatatu.”
32 Amenewa ndiwo anali olembedwa mayina a ana a Isiraeli, malinga ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse olembedwa mayina m’misasa yonse, analipo 603,550.+ 33 Koma Alevi sanawawerenge+ pamodzi ndi ana a Isiraeli enawo, monga Yehova analamulira Mose. 34 Ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.+ Dongosolo limene analitsatira pomanga misasa yawo m’zigawo za mafuko atatu,+ n’limenenso anatsatira posamuka,+ aliyense m’banja lake malinga ndi nyumba ya makolo ake.
3 Nayi mbiri ya mbadwa za Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose m’phiri la Sinai.+ 2 Ana a Aroni mayina awo anali awa: woyamba anali Nadabu, kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+ 3 Amenewa ndiwo anali mayina a ana a Aroni. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anapatsidwa mphamvu* yotumikira monga ansembe.+ 4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova pamene anapereka kwa Yehova moto wosaloleka+ m’chipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Komabe, Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 6 “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+ 7 Iwo ayenera kutumikira iye ndi kutumikiranso khamu lonse pa ntchito za pachihema chokumanako. 8 Azisamalira ziwiya zonse+ za pachihema chokumanako, monga gawo limodzi la ntchito za ana a Isiraeli zimene a fuko la Leviwo aziwagwirira potumikira pachihema chopatulika.+ 9 Aleviwo uwapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera mwa ana a Isiraeli.+ 10 Uike Aroni ndi ana ake kukhala ansembe, kuti azigwira ntchito yaunsembe.+ Aliyense amene si Mlevi akayandikira malowo, aziphedwa.”+
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 12 “Ine ndikutenga Alevi pakati pa ana a Isiraeli m’malo mwa ana onse oyamba kubadwa+ a ana a Isiraeli ndipo iwo akhala anga. 13 Pakuti mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ M’tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo,+ ndinadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
14 Yehova analankhulanso ndi Mose m’chipululu cha Sinai+ kuti: 15 “Uwerenge ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo, malinga ndi mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wamwezi umodzi kupita m’tsogolo.”+ 16 Chotero, Mose anayamba kuwawerenga potsatira mawu a Yehova, monga mmene anamulamulira. 17 Ana a Levi+ anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+
18 Ana a Gerisoni, malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Libini ndi Simeyi.+
19 Ana a Kohati,+ malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Amuramu, Izara,+ Heburoni ndi Uziyeli.
20 Ana a Merari,+ malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+
Awa ndiwo anali mabanja a Alevi, potsata nyumba za makolo awo.
21 Mwa ana a Gerisoni, panali banja la Alibini+ ndi banja la Asimeyi.+ Awa ndiwo anali mabanja a Agerisoni. 22 Amene anawerengedwa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo.+ Onse owerengedwa anakwana 7,500.+ 23 Mabanja a Agerisoni anali kukhala kumbuyo kwa chihema chopatulika.+ Anali kumanga msasa wawo kumadzulo. 24 Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25 Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema chopatulikacho,+ ndi nsalu zake zophimba zosiyanasiyana,+ nsalu yake yotchinga pakhomo,+ 26 nsalu za mpanda+ wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema chopatulika, ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe za chinsalu chake,+ komanso ntchito zonse zokhudza utumikiwu.
27 Mwa ana a Kohati, panali banja la Aamuramu, banja la Aizara, banja la Aheburoni ndi banja la Auziyeli. Awa ndiwo anali mabanja a Akohati.+ 28 Amuna onse owerengedwa, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 8,600. Ntchito ya amenewa inali kutumikira pamalo oyera.+ 29 Mabanja a ana a Kohati anali kumanga msasa wawo kum’mwera kwa chihema chopatulika.+ 30 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31 Ntchito yawo+ inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ndi ziwiya+ za m’malo oyerawo zimene anali kutumikira nazo, ndiponso nsalu yotchinga,+ komanso ntchito zonse zokhudza utumikiwu.
32 Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndiye anali kuyang’anira onse otumikira pamalo oyera.
33 Mwa ana a Merari, panali banja la Amali+ ndi banja la Amusi.+ Awa ndiwo anali mabanja a Amerari.+ 34 Amuna onse owerengedwa, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 6,200.+ 35 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo anali kumanga msasa wawo kumpoto kwa chihema chopatulika.+ 36 Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema chopatulika, mipiringidzo yake,+ mizati yake,+ zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi mizati, ziwiya zonse+ ndi zina zonse zokhudza utumiki umenewu.+ 37 Iwo anali kusamaliranso nsanamira+ za mpanda wozungulira bwalo ndiponso zitsulo zokhazikapo nsanamirazo,+ komanso zikhomo ndi zingwe zake zolimbitsira nsanamirazo.
38 Amene anali kumanga msasa wawo kum’mawa kwa chihema chopatulika, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira m’malo opatulika,+ kutumikira ana a Isiraeli. Aliyense amene si Mlevi akayandikira malowo, anayenera kuphedwa.+
39 Alevi onse amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova, malinga ndi mabanja awo, amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 22,000.
40 Kenako Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Uwerenge ana aamuna onse oyamba kubadwa a Isiraeli, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo,+ ndipo ulembe mayina awo. 41 Unditengere Alevi akhale anga m’malo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa a Isiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi m’malo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za ana a Isiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42 Monga mmene Yehova anamulamulira, Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli. 43 Ndipo ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, anakwana 22,273.
44 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 45 “Unditengere Alevi akhale anga m’malo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli. Unditengerenso ziweto za Alevi zikhale zanga m’malo mwa ziweto za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova. 46 Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47 utenge masekeli* asanu pa munthu aliyense.+ Utenge muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Sekeli limodzi likukwana magera 20.+ 48 Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera ana a Isiraeli otsala poyerekezera ndi chiwerengero cha Alevi.” 49 Chotero, Mose analandira ndalama zowombolera ana a Isiraeli oyamba kubadwa otsala poyerekezera ndi ndalama za dipo la Alevi. 50 Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli, analandira ndalama za masekeli okwanira 1,365, pamuyezo wa sekeli la kumalo oyera. 51 Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, malinga n’zimene Yehova analamula Mose.
4 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Muwerenge ana onse a Kohati+ mwa ana a Levi, malinga ndi mabanja a nyumba za makolo awo. 3 Muwerenge kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ onse olowa m’gulu la ogwira ntchito+ m’chihema chokumanako.
4 “Nawu utumiki wa ana a Kohati m’chihema chokumanako,+ utumiki wopatulika koposa: 5 Pamene msasa ukusamuka, Aroni ndi ana ake azilowa m’chihema. Mmenemo, azichotsa nsalu yotchinga+ n’kuphimba nayo likasa+ la umboni. 6 Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu,*+ n’kuyalanso nsalu yabuluu pamwamba pake. Kenako azibwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+
7 “Iwo aziyala nsalu yabuluu patebulo+ la mkate wachionetsero, n’kuikapo mbale,+ zikho, mbale zolowa,+ ndi mitsuko ya nsembe yachakumwa. Mkate wachionetsero womwe ndi nsembe ya nthawi zonse+ uzikhalabe pomwepo. 8 Akatero, aziziphimba ndi nsalu yowomba ndi ulusi wofiira kwambiri,+ ndiponso aziphimba tebulolo ndi zikopa za akatumbu.+ Kenako azibwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+ 9 Ndiyeno azitenga nsalu yabuluu n’kuphimbira choikapo nyale,+ pamodzi ndi nyale zake,+ zopanira zake zozimitsira nyale,+ zoikamo phulusa la zingwe za nyale,+ ndi ziwiya zake zonse+ zosungiramo mafuta ogwiritsa ntchito nthawi zonse. 10 Choikapo nyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, azichiika m’zikopa za akatumbu+ n’kupisako mtengo wonyamulira. 11 Kenako, aziphimba guwa lansembe+ lagolide ndi nsalu yabuluu. Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu,+ n’kubwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+ 12 Akatero, azitenga ziwiya zonse+ zimene amachitira utumiki wawo nthawi zonse m’malo oyera, n’kuzikuta ndi nsalu yabuluu. Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu,+ n’kuikako mtengo wake wonyamulira.
13 “Ndipo azichotsa phulusa losakanizika ndi mafuta la paguwa lansembe+ n’kuyalapo nsalu ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. 14 Akatero, aziikaponso ziwiya zonse zimene amachitira utumiki paguwapo nthawi zonse. Aziikapo zoikamo phulusa la zingwe za nyale, mafoloko aakulu, mafosholo, mbale zolowa, ndi ziwiya zonse za paguwa lansembe.+ Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, n’kubwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+
15 “Aroni ndi ana ake akamaliza kuphimba zinthu za m’malo oyera+ ndi ziwiya zonse+ za m’malo oyerawo posamutsa msasa, ana a Kohati azilowamo n’kudzazinyamula.+ Iwo asamakhudze+ zinthu za m’malo oyerazo chifukwa angafe. Zinthu zimenezi ndizo katundu wa m’chihema chokumanako amene ana a Kohati azinyamula.+
16 “Eleazara mwana wa wansembe Aroni, aziyang’anira+ mafuta+ a nyale, zofukiza zonunkhira,+ nsembe yanthawi zonse yambewu,+ ndi mafuta odzozera.+ Aziyang’aniranso chihema chonse chopatulika ndi zonse za mmenemo, ndiwo malo oyerawo ndi ziwiya zake.”
17 Yehova analankhulanso ndi Mose ndi Aroni, kuti: 18 “Musalole kuti fuko la mabanja a Akohati+ liwonongeke pakati pa Alevi. 19 Kuti iwo asaphedwe poyandikira zinthu zopatulika koposa,+ koma akhalebe ndi moyo, Aroni ndi ana ake azilowa m’chihemacho. Mmenemo azigawira aliyense wa iwo ntchito ndi katundu woti anyamule. 20 Ana a Kohatiwo asadzayese kulowamo kuti akaone ngakhale pang’ono pokha zinthu zopatulikazo kuti angafe.”+
21 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 22 “Uwerenge ana onse a Gerisoni.+ Uwawerenge potsata nyumba za makolo awo malinga ndi mabanja awo. 23 Uwerenge kuyambira azaka 30 mpaka 50,+ onse olowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako. 24 Tsopano utumiki umene mabanja a Agerisoni azichita ndiponso katundu amene azinyamula ndi uwu:+ 25 Azinyamula nsalu za chihema chopatulika+ ndi chihema chokumanako,+ ndiponso chophimba chake,+ chophimba cha chikopa cha katumbu+ chomwe chili pamwamba pake, ndi nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema chokumanako. 26 Azinyamulanso nsalu za mpanda+ wa bwalo ndi nsalu yotchinga+ khomo la mpanda umene umazungulira chihema chopatulika ndi guwa lansembe. Ndiponso azinyamula zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wawo, pamodzi ndi zinthu zina zonse zogwirira ntchito zawo za nthawi zonse. Umenewu ndiwo utumiki wawo. 27 Ana a Gerisoni+ azichita utumiki wawo wonse molangizidwa ndi Aroni ndi ana ake.+ Aziwauza ntchito zimene azigwira ndi katundu amene azinyamula. Onse muziwagawira katundu amene azinyamula monga gawo lawo. 28 Uwu ndiwo utumiki umene mabanja a ana a Gerisoni+ azichita m’chihema chokumanako. Itamara+ mwana wa wansembe Aroni, ndiye aziyang’anira utumiki wawo.
29 “Ana a Merari+ uwawerenge malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo. 30 Uwerenge kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse olowa m’gulu la ogwira ntchito pachihema chokumanako.+ 31 Tsopano uyu ndi katundu amene azinyamula,+ monga gawo la utumiki wawo m’chihema chokumanako: Mafelemu+ a chihema chopatulika, mipiringidzo yake,+ mizati yake,+ ndiponso zitsulo zokhazikapo mizati ndi mafelemu.+ 32 Azinyamulanso nsanamira+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo nsanamirazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amachitira utumiki wawo. Aliyense muzimugawira katundu woti azinyamula monga gawo lake.+ 33 Uwu ndiwo utumiki wa mabanja a ana a Merari,+ monga gawo la utumiki wawo m’chihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni, ndiye aziyang’anira utumiki wawo.”+
34 Tsopano Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a anthuwo,+ anawerenga ana a Kohati+ malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo. 35 Anawerenga kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ onse amene analowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako.+ 36 Onse owerengedwa, malinga ndi mabanja awo, anakwana 2,750.+ 37 Awa ndiwo anawerengedwa+ mwa mabanja a ana a Kohati, onse otumikira m’chihema chokumanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova kwa Mose.
38 Onse owerengedwa mwa ana a Gerisoni,+ malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, 39 kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse amene analowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako,+ 40 amene anawerengedwa malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, onse pamodzi anakwana 2,630.+ 41 Amenewa ndiwo anawerengedwa mwa mabanja a ana a Gerisoni, onse otumikira m’chihema chokumanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova.+
42 Onse owerengedwa mwa mabanja a ana a Merari, malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, 43 kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse olowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako,+ 44 amene anawerengedwa malinga ndi mabanja awo, onse pamodzi anakwana 3,200.+ 45 Amenewa ndiwo anawerengedwa mwa mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova kwa Mose.+
46 Alevi onse owerengedwa, amene Mose ndi Aroni limodzi ndi atsogoleri a Isiraeli anawawerenga, malinga ndi mabanja awo potsata nyumba za makolo awo, 47 kuyambira azaka 30 mpaka 50,+ onse ogwira ntchito yolemetsa ndi utumiki wonyamula katundu m’chihema chokumanako,+ 48 onse owerengedwawo anakwana 8,580.+ 49 Pomvera mawu a Yehova, Mose anawawerenga, aliyense malinga ndi utumiki wake ndi katundu wake wonyamula. Anawerengedwa monga mmene Yehova analamulira Mose.+
5 Popitiriza kulankhula ndi Mose, Yehova anati: 2 “Lamula ana a Isiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche,+ ndi aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu.+ 3 Kaya akhale mwamuna kapena mkazi, uziwatulutsa kunja kwa msasa+ kuti asadetse+ misasa ya anthu amene ine ndikukhala pakati pawo.”+ 4 Ana a Isiraeli anali kuchitadi zimenezo. Anali kutulutsadi anthuwo kunja kwa msasa, monga mmene Yehova anauzira Mose.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 6 “Lankhula kwa ana a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna kapena mkazi akachita machimo alionse amene anthu amachita, kuchimwira Yehova, iyenso azikhala ndi mlandu.+ 7 Munthuyo aziulula+ tchimo lake limene wachita. Azipereka malipiro onse a mlandu wake, komanso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu a malipirowo.+ Azipereka malipirowo kwa munthu amene wam’lakwira. 8 Koma ngati wolakwiridwayo wamwalira wopanda wachibale wake weniweni, amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aperekedwe kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Wochimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo am’phimbire machimo ake.+
9 “‘Zopereka zonse+ za zinthu zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa wansembe, zizikhala zake.+ 10 Zinthu zopatulika zimene munthu aliyense azipereka, zizikhala za wansembe. Chilichonse chimene munthu angapereke kwa wansembe, chimenecho chizikhala chake.’”
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mkazi wa munthu angazembere mwamuna wake n’kumuchimwira+ 13 mwakuti mwamuna wina wagona* naye,+ koma zimenezi n’kukhala zobisika kwa mwamuna wake.+ Ngakhale kuti mkaziyo wadziipitsa ndithu, zingachitike kuti palibe munthu amene angapereke umboni wotsimikizira kuti mkaziyo walakwadi ndipo iye sanagwidwe. 14 Koma mwamuna wake akhoza kukhala ndi nsanje+ mumtima mwake, n’kumaganiza kuti mkaziyo sanayende bwino, pamene mkaziyo wadziipitsadi. Kapena mwamuna akhoza kukhala ndi nsanje mumtima mwake n’kumaganiza kuti mkazi wake sanayende bwino, pamene mkaziyo sanadziipitse. 15 Mulimonsemo, mwamunayo azitenga mkaziyo n’kupita naye kwa wansembe.+ Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani,*+ chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yachikumbutso, yokumbutsa cholakwa.
16 “‘Wansembeyo azitenga mkaziyo n’kumuimiritsa pamaso pa Yehova.+ 17 Wansembeyo azitenga madzi opatulika m’chiwiya chadothi. Azitengakonso fumbi lapansi m’chihema chopatulika, n’kulithira m’madziwo. 18 Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova n’kumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ n’kuiika m’manja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga m’dzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+
19 “‘Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo, pomuuza kuti: “Ngati mwamuna aliyense sanagone nawe, ndipo ngati sunam’zembere mwamuna wako pamene uli m’manja mwake,+ n’kuchita chodetsa chilichonse, madzi owawa obweretsa tembererowa asakuvulaze. 20 Koma ngati unazembera mwamuna wako pamene uli m’manja mwake,+ mwa kudziipitsa, mwakuti mwamuna wina wagona nawe,*+ . . . ” 21 Tsopano wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro la temberero.+ Iye aziti kwa mkaziyo: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu amtundu wako. Yehova achite zimenezo mwa kufotetsa ntchafu*+ yako, ndi kutupitsa mimba yako. 22 Madzi a tembererowa alowe m’matumbo mwako kuti akatupitse mimba yako ndi kufotetsa ntchafu yako.” Ndipo mkaziyo aziyankha kuti: “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”*
23 “‘Wansembeyo azilemba matemberero amenewa m’buku+ ndi kuwafafaniza+ m’madzi owawa aja. 24 Azimwetsa mkaziyo madzi owawa a tembererowo,+ ndipo madziwo akalowa m’thupi mwake, mkaziyo azimva ululu. 25 Ndiyeno wansembeyo azitenga nsembe yambewu+ yansanje imene ili m’manja mwa mkaziyo, ndi kuiweyulira uku ndi uku pamaso pa Yehova. Akatero, aziibweretsa pafupi ndi guwa lansembe. 26 Wansembeyo azitapako nsembe yambewuyo monga chikumbutso,+ n’kuifukiza paguwa lansembe. Pambuyo pake, azipatsa mkaziyo madziwo kuti amwe. 27 Akam’mwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa mwa kugona ndi mwamuna wina,+ madzi a tembererowo akalowa m’thupi mwake, azikhala chinthu chowawa. Pamenepo mimba yake izitupa, ndipo ntchafu yake izifota. Mkaziyo azikhala chitsanzo cha wotembereredwa pakati pa anthu amtundu wake.+ 28 Koma ngati mkaziyo ali woyera chifukwa sanadziipitse, chilangocho chisam’gwere,+ ndipo azitha kutenga pakati.
29 “‘Limeneli ndilo lamulo la nkhani ya nsanje,+ pamene mkazi wazembera mwamuna wake,+ n’kudziipitsa pamene ali m’manja mwake,+ 30 kapena pamene mwamuna wakhala ndi nsanje mumtima mwake, ndipo akuganiza kuti mkazi wake sanayende bwino. Zikatero, mwamunayo aziimiritsa mkazi wake pamaso pa Yehova, ndipo wansembe azichita zonse zofunika pa mkaziyo malinga ndi lamulo limeneli. 31 Mwamunayo adzakhala wopanda cholakwa, koma mkaziyo adzalandira chilango cha kulakwa kwake.’”
6 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Munthu aliyense, mwamuna kapena mkazi, akachita lonjezo lapadera lokhala Mnaziri+ kwa Yehova, 3 azisala vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa.+ Asamamwe ngakhale viniga* wochokera ku vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa, kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma. 4 Masiku ake onse okhala Mnaziri, asamadye chilichonse chochokera ku mtengo wa mpesa, kaya zikhale mphesa zosapsa kapena khungu lake.
5 “‘Masiku onse a lonjezo lake lokhala Mnaziri, lezala lisadutse kumutu kwake+ kufikira atatha masiku ake amene anadzipereka kwa Yehova. Azikhala woyera mwa kusiya tsitsi+ lake la kumutu kuti likule. 6 Masiku onse amene iye ali wodzipereka kwa Yehova, asamakhudze mtembo.+ 7 Asadziipitse pokhudza ngakhale mtembo wa bambo ake, mayi ake, m’bale wake kapena mlongo wake, iwo akamwalira.+ Asadziipitse nawo chifukwa chizindikiro cha unaziri wake kwa Mulungu chili kumutu kwake.
8 “‘Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake. 9 Koma ngati munthu wina wafera pambali pake mwadzidzidzi,+ moti Mnaziriyo waipitsa mutu umene uli ndi chizindikiro cha unaziri wake pokhudza mtembowo, amete tsitsi+ la kumutu kwake pa tsiku la kuyeretsedwa kwake. Alimete pa tsiku la 7. 10 Ndipo pa tsiku la 8, abweretse ana a njiwa awiri, kapena ana a nkhunda awiri kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+ 11 Wansembeyo atenge mwana mmodzi wa njiwa kapena wa nkhunda n’kumupereka monga nsembe yamachimo.+ Atengenso mwana wa njiwa kapena wa nkhunda winayo n’kumupereka monga nsembe yopsereza.+ Achite zimenezi kuti aphimbe machimo a munthuyo, popeza wachimwa pokhudza mtembo. Akatero aziyeretsa mutu wake pa tsikulo. 12 Munthuyo ayambirenso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri,+ ndipo abweretse nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe ya kupalamula.+ Masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anaipitsa unaziri wake.
13 “‘Nali lamulo lokhudza Mnaziri: Pa tsiku limene masiku a unaziri wake atha,+ amubweretse pakhomo la chihema chokumanako. 14 Ndipo apereke kwa Yehova nsembe ya iye mwini. Nsembeyo ikhale nkhosa yaing’ono yamphongo yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yopsereza.+ Aperekenso mwana wa nkhosa wamkazi wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ Komanso apereke nkhosa yamphongo yopanda chilema, monga nsembe yachiyanjano.+ 15 Aperekenso dengu la mikate yozungulira yoboola pakati. Mikateyo ikhale yopanda chofufumitsa, yophika ndi ufa wosalala,+ ndi yopaka mafuta.+ M’dengumo mukhalenso timikate topyapyala topanda chofufumitsa topaka mafuta,+ limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ 16 Wansembeyo abweretse zinthuzo pamaso pa Yehova, ndipo am’perekere nsembe yake yamachimo ndi nsembe yake yopsereza.+ 17 Am’perekerenso nkhosa yamphongo monga nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, limodzi ndi dengu la mikate yopanda chofufumitsa ija. Kenako, wansembeyo apereke nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa, zimene zimayendera limodzi ndi nsembe yachiyanjanoyo.
18 “‘Mnaziriyo azimeta tsitsi+ la kumutu kwake, lomwe ndi chizindikiro cha unaziri wake. Azilimetera pakhomo la chihema chokumanako. Akatero, azitenga tsitsi la mutu wake wa unazirilo, n’kuliponya pamoto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano. 19 Wansembe atenge mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Atengenso m’dengumo mkate woboola pakati wopanda chofufumitsa, ndi kamkate kopyapyala kopanda chofufumitsa.+ Zinthuzi aziike m’manja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake. 20 Tsopano wansembeyo aweyulire* zinthuzo uku ndi uku monga nsembe yoweyula kwa Yehova.+ Zinthuzi zipite kwa wansembeyo ngati mphatso yopatulika, limodzi ndi nganga+ ya nsembe yoweyulayo, komanso mwendo umene aupatula kuti ukhale chopereka.+ Pambuyo pake yemwe anali Mnaziriyo angathe kumwa vinyo.+
21 “‘Limeneli ndilo lamulo kwa Mnaziri+ amene anachita lonjezo, lamulo lokhudza nsembe zimene ayenera kupereka kwa Yehova, kupatula zina zowonjezera zimene angathe kupereka mwa iye yekha. Achite mogwirizana ndi lonjezo lake, popeza ndilo lamulo la unaziri wake.’”
22 Kenako Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 23 “Lankhula ndi Aroni ndiponso ana ake kuti, ‘Muzidalitsa+ ana a Isiraeli motere:
24 “Yehova akudalitseni+ ndi kukusungani.+
25 Yehova akukomereni mtima,+ ndipo akuyanjeni.+
26 Yehova akuyang’aneni mokondwera+ ndipo akupatseni mtendere.”’+
27 Aroni ndi ana ake amveketse dzina langa+ pakati pa ana a Isiraeli kuti ndiwadalitse.”+
7 Pa tsiku limene Mose anamaliza kumanga chihema chopatulika,+ anachidzoza+ n’kuchipatula, limodzi ndi zipangizo zake zonse, komanso guwa lansembe ndi ziwiya zake zonse. Zonse anazidzoza n’kuzipatula.+ 2 Pamenepo atsogoleri a Isiraeli,+ amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anapereka zopereka zawo.+ Anatero monga atsogoleri a mafuko awo, monganso oyang’anira anthu amene anawerengedwa aja. 3 Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova. Zoperekazo zinali ngolo 6 zotseka pamwamba, ndi ng’ombe 12. Zimenezi zikutanthauza kuti atsogoleri awiri anapereka ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense anapereka ng’ombe yamphongo imodzi. Zoperekazo anafika nazo pachihema chopatulika. 4 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: 5 “Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zikhale zogwiritsa ntchito pa utumiki wa pachihema chokumanako. Uzipereke kwa Alevi, aliyense malinga ndi utumiki wake.”
6 Choncho Mose analandira ngolo ndi ng’ombezo, n’kuzipereka kwa Alevi. 7 Anapereka ngolo ziwiri ndi ng’ombe zinayi kwa ana a Gerisoni, malinga ndi utumiki wawo.+ 8 Ana a Merari anawapatsa ngolo zinayi ndi ng’ombe 8, malinga ndi utumiki wawo+ umene anali kuchita moyang’aniridwa ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.+ 9 Koma ana a Kohati sanawagawire zinthuzo, chifukwa utumiki wawo unali wonyamula zinthu za pamalo oyera,+ ndipo anali kuzinyamulira paphewa.+
10 Tsopano atsogoleriwo anafika ndi zopereka zawo pamwambo wotsegulira guwa lansembe,+ pa tsiku lodzoza guwalo. Anabweretsa zopereka zawozo kuguwa lansembe. 11 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kaperekedwe ka zopereka zotsegulira guwalo kakhale kotere, pa tsiku limodzi mtsogoleri mmodzi azipereka zopereka zake.”+
12 Amene anapereka zopereka zake pa tsiku loyamba anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda. 13 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 14 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 15 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 16 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 17 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Naasoni, mwana wa Aminadabu.+
18 Netaneli+ mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, anapereka zopereka zake pa tsiku lachiwiri. 19 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 20 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 21 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 22 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 23 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Netaneli mwana wa Zuwara.
24 Pa tsiku lachitatu panali mtsogoleri wa ana a Zebuloni, Eliyabu+ mwana wa Heloni. 25 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu. 26 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 27 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 28 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 29 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Eliyabu mwana wa Heloni.+
30 Pa tsiku lachinayi panali mtsogoleri wa ana a Rubeni, Elizuri+ mwana wa Sedeuri. 31 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 32 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 33 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 34 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 35 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Elizuri mwana wa Sedeuri.+
36 Pa tsiku lachisanu panali mtsogoleri wa ana a Simiyoni, Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai. 37 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 38 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 39 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 40 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 41 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Selumiyeli mwana wa Zurisadai.+
42 Pa tsiku la 6 panali mtsogoleri wa ana a Gadi, Eliyasafu+ mwana wa Deyueli. 43 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 44 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10 chodzaza ndi zofukiza.+ 45 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 46 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 47 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Eliyasafu mwana wa Deyueli.+
48 Pa tsiku la 7 panali mtsogoleri wa ana a Efuraimu, Elisama+ mwana wa Amihudi. 49 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 50 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 51 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 52 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 53 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Elisama mwana wa Amihudi.+
54 Pa tsiku la 8 panali mtsogoleri wa ana a Manase, Gamaliyeli+ mwana wa Pedazuri. 55 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 56 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 57 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 58 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 59 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.+
60 Pa tsiku la 9 panali mtsogoleri+ wa ana a Benjamini, Abidana+ mwana wa Gidoni. 61 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 62 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 63 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 64 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 65 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Abidana mwana wa Gidoni.+
66 Pa tsiku la 10 panali mtsogoleri wa ana a Dani, Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai. 67 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 68 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 69 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 70 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 71 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Ahiyezeri mwana wa Amisadai.+
72 Pa tsiku la 11 panali mtsogoleri wa ana a Aseri, Pagiyeli+ mwana wa Okirani. 73 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 74 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 75 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 76 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 77 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Pagiyeli mwana wa Okirani.+
78 Pa tsiku la 12 panali mtsogoleri wa ana a Nafitali, Ahira+ mwana wa Enani. 79 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 80 Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 81 Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 82 Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 83 Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Ahira mwana wa Enani.+
84 Potsegulira guwa lansembe,+ pa tsiku limene guwalo linadzozedwa, atsogoleri+ a Isiraeli anapereka izi: Mbale zikuluzikulu zasiliva 12, mbale zolowa zasiliva+ 12, zikho zagolide 12. 85 Mbale yaikulu iliyonse yasiliva inali yolemera masekeli 130, ndipo mbale yolowa iliyonse inali yolemera masekeli 70. Siliva yense wa ziwiya zonsezi anali wolemera masekeli 2,400, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera.+ 86 Anaperekanso zikho 12 zagolide+ zodzaza ndi zofukiza. Chikho chilichonse chinali cholemera masekeli 10, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Golide yense wa zikho zonsezi anali wolemera masekeli 120. 87 Nyama zonse zoperekedwa za nsembe yopsereza+ zinalipo ng’ombe 12 zamphongo, nkhosa 12 zamphongo, ndi ana a nkhosa 12 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zinaperekedwa limodzi ndi nsembe zawo zambewu.+ Atsogoleriwa anaperekanso ana a mbuzi 12 a nsembe yamachimo.+ 88 Nyama zonse zoperekedwa za nsembe yachiyanjano+ zinalipo ng’ombe 24 zamphongo, nkhosa 60 zamphongo, mbuzi 60 zamphongo, ndi ana a nkhosa 60 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinaperekedwa pamwambo+ wotsegulira guwa lansembe, pambuyo poti ladzozedwa.+
89 Nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri.+ Mulungu anali kulankhula naye motero.
8 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 2 “Lankhula ndi Aroni, unene kuti, ‘Ukayatsa nyale 7 zija, ziziunika malo apatsogolo pa choikapo nyalecho.’”+ 3 Ndipo Aroni anayamba kuchitadi zimenezo. Anayatsa nyalezo kuti ziwalitse malo apatsogolo pa choikapo nyalecho,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 4 Choikapo nyalecho chinali chooneka motere kapangidwe kake: Chinali chosula, chagolide. Chinasulidwa kuchokera kutsinde lake mpaka kumaluwa ake.+ Anachisula malinga ndi chitsanzo chimene Yehova anaonetsa+ Mose m’masomphenya.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 6 “Tenga Alevi pakati pa ana a Isiraeli, ndipo uwayeretse.+ 7 Kuwayeretsa kwake uchite motere: Uwawaze madzi oyeretsera machimo,+ ndipo iwo amete thupi lonse.+ Komanso achape zovala zawo+ kuti akhale oyera.+ 8 Kenako iwo atenge ng’ombe yaing’ono yamphongo,+ pamodzi ndi nsembe yake yambewu+ ya ufa wosalala wothira mafuta. Iweyo utenge ng’ombe inanso yaing’ono yamphongo ya nsembe yamachimo.+ 9 Ukatero, ubweretse Aleviwo kuchihema chokumanako, ndipo usonkhanitse khamu lonse la ana a Isiraeli.+ 10 Ndiyeno upereke Aleviwo pamaso pa Yehova, ndipo ana a Isiraeliwo aike+ manja awo pa Aleviwo.+ 11 Pamenepo, Aroni auze Aleviwo kuti ayende uku ndi uku pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula*+ ya ana a Isiraeli. Iwo azigwira ntchito yotumikira Yehova.+
12 “Aleviwo aike manja awo pamitu ya ng’ombe zamphongozo.+ Pambuyo pake, upereke kwa Yehova ng’ombe imodzi monga nsembe yamachimo, ndipo inayo uipereke monga nsembe yopsereza yophimbira machimo+ a Alevi. 13 Uimiritse Aleviwo pamaso pa Aroni ndi ana ake, ndi kuwauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula kwa Yehova. 14 Upatule Aleviwo pakati pa ana a Isiraeli kuti akhale anga.+ 15 Pambuyo pake, Aleviwo azitumikira pachihema chokumanako.+ Chotero uwayeretse, ndi kuwauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula.+ 16 Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndikuwatenga iwowa m’malo mwa onse otsegula mimba ya mayi awo, oyamba kubadwa onse pakati pa ana a Isiraeli.+ 17 Mwana woyamba kubadwa aliyense pakati pa ana a Isiraeli ndi wanga, kaya akhale wa munthu kapena wa nyama.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana woyamba kubadwa aliyense m’dziko la Iguputo+ ndinawapatula kuti akhale anga.+ 18 Choncho m’malo mwa ana oyamba kubadwa onse a Isiraeli, ndikutenga Alevi kuti akhale anga.+ 19 Ndipo ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa ana a Isiraeli.+ Aleviwo adzatumikira m’malo mwa ana a Isiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a ana a Isiraeli.+ Chifukwa cha utumiki wawowo, mliri sudzawagwera ana a Isiraeli pakuti sadzayandikira malo oyerawo.”
20 Choncho Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Isiraeli, anachita zonse zofunikira kwa Alevi. Ana a Isiraeliwo anachitira Aleviwo malinga ndi zonse zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 21 Aleviwo anadziyeretsa+ n’kuchapa zovala zawo. Pambuyo pake, Aroni anawauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.+ Kenako Aroniyo anawaphimbira machimo awo kuti awayeretse.+ 22 Ndiyeno Aleviwo analowa n’kukayamba utumiki wawo m’chihema chokumanako, pamaso pa Aroni ndi ana ake.+ Anthu anachitira Aleviwo malinga ndi zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi.
23 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 24 “Lamulo lokhudza Alevi ndi ili: Kuyambira wazaka 25 kupita m’tsogolo azilowa m’gulu la otumikira m’chihema chokumanako. 25 Koma akakwanitsa zaka 50 atuluke m’gululo, ndipo asadzatumikirenso. 26 Iye azingothandizira abale ake m’chihema chokumanako pochita utumiki wawo, koma asatumikire. Umu ndi mmene uzichitira ndi Alevi malinga ndi ntchito zawo.”+
9 M’mwezi woyamba*+ wa chaka chachiwiri, ana a Isiraeli atatuluka m’dziko la Iguputo, Yehova analankhula ndi Mose m’chipululu cha Sinai. Iye anati: 2 “Tsopano ana a Isiraeli akonze nsembe ya pasika+ pa nthawi yake yoikidwiratu.+ 3 Mukonze nsembeyo pa tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo kuli kachisisira,*+ ndiyo nthawi yake yoikidwiratu. Muikonze malinga ndi malamulo ake onse, ndiponso motsatira njira zonse za kakonzedwe kake.”+
4 Pamenepo Mose analankhula kwa ana a Isiraeli kuti akonze nsembe ya pasika. 5 Iwo anakonza nsembe ya pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, madzulo kuli kachisisira, m’chipululu cha Sinai. Ana a Isiraeliwo anachita zonse malinga ndi zimene Yehova analamula Mose.+
6 Tsopano panali amuna ena amene anadzidetsa pokhudza mtembo wa munthu,+ moti sanathe kukonza nsembe ya pasika pa tsikulo. Chotero anakaonekera kwa Mose ndi Aroni pa tsikulo.+ 7 Ndipo iwo ananena kuti: “Ife ndife odetsedwa chifukwa takhudza mtembo wa munthu. Ngakhale kuti zili choncho, kodi tiyeneradi kuletsedwa kupereka nsembe+ kwa Yehova pakati pa ana a Isiraeli pa nthawi yake yoikidwiratu?” 8 Pamenepo Mose anawayankha kuti: “Dikirani pomwepo, ndimve zimene Yehova ati alamule zokhudza inu.”+
9 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 10 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu wina aliyense mwa inu kapena mwa mbadwa zanu, amene wadetsedwa pokhudza mtembo wa munthu,+ kapena amene ali pa ulendo wautali, akonzebe nsembe ya pasika yopereka kwa Yehova. 11 Azikonza nsembeyo m’mwezi wachiwiri+ pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira. Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa, ndiponso masamba owawa.+ 12 Pasatsaleko iliyonse yoti ifike m’mawa,+ ndipo asaphwanye fupa lake lililonse.+ Aikonze motsatira malamulo onse a pasika.+ 13 Koma ngati munthu ali wosadetsedwa, kapena sanapite pa ulendo, ndipo wanyalanyaza kukonza nsembe ya pasika, munthuyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake,+ chifukwa sanapereke nsembeyo kwa Yehova pa nthawi yake yoikidwiratu. Munthuyo adzafa chifukwa cha kuchimwa kwake.+
14 “‘Ngati pali mlendo amene akukhala pakati panu, iyenso azikonza nsembe ya pasika yopereka kwa Yehova.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a pasika, ndiponso kakonzedwe kake ka nthawi zonse.+ Pakhale malamulo ofanana kwa nonsenu, kaya mlendo kapena mbadwa.’”+
15 Pa tsiku lomanga chihema chopatulika,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho.+ Koma kuyambira madzulo mpaka m’mawa, moto+ unali kuoneka pamwamba pa chihema chopatulikacho. 16 Zinali kuchitika motero nthawi zonse. Mtambo unali kuima pamwamba pa chihemacho masana, ndipo usiku moto unali kuonekera pamwamba pake.+ 17 Mtambowo ukanyamuka pamwamba pa chihemacho, ana a Isiraeli anali kunyamuka nthawi yomweyo.+ Ndipo pamalo pamene mtambowo waima, m’pamene ana a Isiraeli anali kumangapo msasa.+ 18 Choncho Yehova akalamula, ana a Isiraeli anali kunyamuka, ndipo Yehova akalamula, anali kumanga msasa.+ Masiku onse amene mtambo unali pamwamba pa chihemacho, iwo anali kukhalabe pamsasapo. 19 Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihema, ana a Isiraeli ankamverabe Yehova, ndipo sankachoka pamalopo.+ 20 Nthawi zina mtambowo unali kungokhala masiku owerengeka pamwamba pa chihemapo. Yehova akalamula,+ iwo anali kukhalabe pamsasapo, ndipo Yehova akalamula, iwo anali kuchoka. 21 Nthawi zina mtambowo+ unali kukhalapo kuchokera madzulo kufika m’mawa, ndipo m’mawawo mtambowo unali kuchoka, anthuwo n’kunyamuka. Kaya mtambowo uchoke masana kapena usiku, iwonso anali kunyamuka.+ 22 Kaya mtambowo ukhale pamwamba pa chihemacho masiku awiri, mwezi, kapena masiku ambiri, ana a Isiraeli anali kukhalabe pamsasa osachoka. Koma mtambowo ukanyamuka, iwo anali kuchoka.+ 23 Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka.+ Anali kumvera Yehova potsatira malangizo a Yehova odzera kwa Mose.+
10 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 2 “Upange malipenga+ awiri asiliva. Uchite kusula, ndipo uziwagwiritsa ntchito poitanitsa+ msonkhano ndi posamutsa msasa. 3 Akaliza malipenga onse awiriwo, khamu lonse lizisunga pangano la msonkhano ndi iwe, ndipo lizifika pakhomo la chihema chokumanako.+ 4 Koma akaliza lipenga limodzi lokha, akuluakulu amene ndi atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, nawonso azisunga pangano la msonkhano ndi iwe.+
5 “Mukaliza lipenga lolira mosinthasintha, a m’misasa yakum’mawa+ azinyamuka ulendo. 6 Mukaliza kachiwiri lipenga lolira mosinthasintha, a m’misasa yakum’mwera+ azinyamuka ulendo. Gulu lililonse likamanyamuka, aziliza lipenga lolira mosinthasintha.
7 “Poitanitsa msonkhano wa anthu onse muziliza lipenga,+ koma osati lolira mosinthasintha. 8 Ana a Aroni, ansembewo, ndiwo aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kugwiritsa ntchito malipengawa m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.*
9 “Adani okuvutitsani akakuukirani+ kuti akuthireni nkhondo m’dziko lanu, muziliza malipengawo+ moitanira asilikali kunkhondo. Mukatero, Mulungu wanu Yehova adzakukumbukirani ndithu ndi kukupulumutsani kwa adani anuwo.+
10 “Pa tsiku lanu losangalala,+ pa nyengo ya zikondwerero zanu,+ ndi pa masiku oyambira miyezi,+ muziliza malipengawo popereka nsembe zanu zopsereza+ ndi zachiyanjano.+ Kuliza malipengawo kudzakhala chikumbutso kwa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”+
11 Tsopano m’chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12 Nawonso ana a Isiraeli ananyamuka mwa dongosolo lawo lonyamukira.+ Ananyamuka m’chipululu cha Sinai, ndipo mtambowo unakaima m’chipululu cha Parana.+ 13 Iwo anasamuka malinga ndi malangizo amene Yehova anapereka kudzera kwa Mose.+ Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke.
14 Choncho, a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Yuda ndiwo anayamba kunyamuka m’magulu awo.+ Mtsogoleri wa asilikali awo anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 15 Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Isakara anali Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 16 Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Zebuloni anali Eliyabu, mwana wa Heloni.+
17 Chihema chopatulika chitapasulidwa,+ ana a Gerisoni+ ndi ana a Merari,+ onyamula chihema chopatulikacho, ananyamuka.
18 Kenako, a m’chigawo cha mafuko atatu cha Rubeni+ ananyamuka m’magulu awo. Mtsogoleri wa asilikali awo anali Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 19 Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Simiyoni+ anali Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 20 Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Gadi anali Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli.
21 Kenako Akohati, onyamula zinthu za m’malo opatulika+ ananyamuka, kuti pokafika akapeze chihema chopatulika chitamangidwa kale.
22 Ndiyeno a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Efuraimu+ ananyamuka m’magulu awo. Mtsogoleri wa asilikali awo anali Elisama,+ mwana wa Amihudi. 23 Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Manase+ anali Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 24 Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Benjamini+ anali Abidana,+ mwana wa Gidoni.
25 Pomaliza, a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Dani+ ananyamuka. Iwo ndiwo anali olonda kumbuyo kwa zigawo zonse za mafukowo.+ Mtsogoleri wa asilikali awo anali Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26 Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Aseri+ anali Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 27 Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Nafitali+ anali Ahira,+ mwana wa Enani. 28 Ili ndilo dongosolo limene ana a Isiraeli anali kulitsatira posamuka m’magulu awo.+
29 Ndiyeno Mose anauza Hobabu yemwe anali mwana wa Reueli+ Mmidiyani, mpongozi wake kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino ndithu,+ pakuti Yehova analonjeza Aisiraeli zabwino.”+ 30 Koma iye anamuyankha kuti: “Ayi, sindipita nanu kumeneko. Ndikubwerera kudziko lakwathu,+ kwa abale anga.” 31 Komabe Mose anam’pempha kuti: “Chonde musatisiye, pakuti inu mukudziwa bwino kumene tingamange msasa m’chipululu muno, ndipo mungakhale maso athu. 32 Mukapita nafe limodzi,+ popeza Yehova adzatichitira zabwino, ifenso tidzakuchitirani zabwino.”
33 Chotero iwo ananyamuka kuphiri la Yehova,+ n’kuyenda ulendo wa masiku atatu. Likasa la pangano la Yehova+ linali patsogolo pawo ulendo wa masiku atatu wonsewo, kuwafunira malo oti amangepo msasa.+ 34 Akanyamuka pamsasa masana, mtambo wa Yehova+ unali pamwamba pawo.
35 Nthawi zonse likasa likamanyamuka, Mose anali kunena kuti: “Nyamukani, inu Yehova, adani anu abalalike.+ Ndipo amene ali nanu chidani chachikulu athawe patsogolo panu.”+ 36 Nthawi zonse likasalo likaima, iye ankati: “Bwererani inu Yehova, kumiyandamiyanda yosawerengeka ya Aisiraeli.”+
11 Tsopano anthuwo anayamba kudandaula pamaso pa Yehova ngati kuti anali pamavuto.+ Yehova atamva kudandaulako anawapsera mtima, ndipo moto wa Yehova unawayakira n’kupsereza ena a iwo kumalire a msasa.+ 2 Koma pamene anthuwo anayamba kulirira Mose, iye anapembedzera Yehova+ ndipo motowo unazima. 3 Malo amenewo anawatcha Tabera,*+ chifukwa moto wa Yehova unawayakira pamalo amenewo.
4 Tsopano khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ lomwe linali pakati pawo linasonyeza mtima wadyera,+ ndipo ana a Isiraeli nawonso anayamba kulira n’kumanena kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye?+ 5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinali kudya ku Iguputo,+ nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu! 6 Koma tsopano tilibe ndi mphamvu zomwe. Maso athu sakuonanso kanthu kena, koma mana basi.”+
7 Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo maonekedwe ake anali ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi.+ 8 Anthuwo anali kumwazikana kukatola manawo.+ Akatero, ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo. Kenako ankawawiritsa mumphika,+ kapena kuwapanga makeke ozungulira. Kukoma kwake anali ngati keke yotsekemera* yothira mafuta.+ 9 Mame akagwa pamsasa usiku, mananso ankagwa.+
10 Tsopano Mose anamva anthu akulira m’mabanja mwawo, munthu aliyense pakhomo la hema wake. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unawayakira koopsa anthuwo.+ Mose nayenso anaipidwa nazo zimenezo.+ 11 Ndiyeno Mose anadandaulira Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mwandivutitsa chonchi ine mtumiki wanu? N’chifukwa chiyani mwandiumira mtima chotere, n’kundisenzetsa chimtolo cha anthu onsewa?+ 12 Kodi ndine ndinatenga pakati pa anthu onsewa? Ndine kodi ndinawabereka, kuti mundiuze kuti, ‘Uwafukate pachifuwa chako+ mmene mlezi amafukatira mwana woyamwa,’+ pa ulendo wopita nawo kudziko limene munalumbirira makolo awo?+ 13 Ndiitenga kuti nyama yoti ndipatse anthu onsewa? Pakuti iwo akupitirizabe kundilirira ine, kuti, ‘Tipatse nyama yoti tidye!’ 14 Sindingathe kuwasamalira ndekha anthuwa, chifukwa iwo ndi chimtolo chimene sindingathe kuchisenza.+ 15 Ngati umu ndi mmene muchitire ndi ine, ndikomereni mtima chonde, ingondiphani kuti tsokali lindichoke.”+
16 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Undisonkhanitsire akulu 70 mwa akulu a Isiraeli,+ amene ukuwadziwa kuti ndiwo akulu ndi oyang’anira pakati pa anthuwo.+ Upite nawo kuchihema chokumanako, ndipo akaime kumeneko limodzi nawe. 17 Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+ 18 Ndipo uuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera tsiku lamawa,+ pakuti mudya nyama. Paja mwakhala mukulirira Yehova,+ kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye? Ku Iguputo zinthu zinali kutiyendera bwino.”+ Nyamayo Yehova akupatsani ndithu, ndipo muidyadi.+ 19 Imeneyo simuidya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku 10, kapenanso masiku 20 ayi, 20 koma mudzaidya kwa mwezi wonse wathunthu, mpaka idzatulukira m’mphuno mwanu, ndipo mudzachita kunyansidwa nayo.+ Zidzatero chifukwa mwakana Yehova amene ali pakati panu, ndipo mukum’lirira kuti: “Tinachokeranji ku Iguputo?”’”+
21 Koma Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo akukwana 600,000,+ koma inuyo mukunena kuti, ‘Nyamayo ndiwapatsa, ndipo adzaidya kwa mwezi wonse wathunthu.’ 22 Kodi tiwaphera ziweto zonse kuti ziwakwanire?+ Kapena tiwaphera nsomba zonse za m’nyanja kuti ziwakwanire?”
23 Ndiyeno Yehova anamuyankha Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova lafupika lero eti?+ Tsopano uona ngati zimene ndanena zichitikedi kapena ayi.”+
24 Pamenepo Mose anapita kukauza anthuwo mawu a Yehova. Anasonkhanitsa amuna 70 kuchokera pa akulu a anthuwo, n’kuwauza kuti aimirire mozungulira chihema chokumanako.+ 25 Kenako Yehova anatsika mumtambo+ n’kulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose n’kuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri, koma sanadzachitenso kachiwiri.+
26 Tsopano panali amuna awiri amene anatsalira mumsasa. Wina dzina lake anali Eledadi, ndipo winayo anali Medadi. Mzimuwo unatsika pa amenewanso, chifukwa anali pakati pa olembedwawo, ngakhale kuti sanapite nawo kuchihema chokumanako kuja. Choncho iwonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri mumsasamo. 27 Pamenepo mnyamata wina anathamanga kukanena kwa Mose, kuti: “Eledadi ndi Medadi akuchita zinthu ngati aneneri mumsasa.” 28 Pamenepo, Yoswa mwana wa Nuni, yemwe anali mtumiki+ wa Mose kuyambira ali mnyamata, anayankhira kuti: “Mbuyanga Mose, kawaletseni amenewo!”+ 29 Koma Mose anayankha kuti: “Kodi ukuchita nsanje chifukwa chondidera nkhawa? Ayi usatero. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneri, chifukwa Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!”+ 30 Pambuyo pake, Mose limodzi ndi akulu a Isiraeliwo anabwerera kumsasa.
31 Kenako Yehova anautsa mphepo+ yamkokomo kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri,+ ndipo inazimwaza kuyambira pamsasapo mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali ina, ndiponso mtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali inayo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinali kuuluka m’munsi kwambiri pafupifupi mikono* iwiri kuchokera pansi. 32 Ndiyeno anthuwo anayamba kugwira zinzirizo. Anazigwira masana onse mpaka usiku wonse, mpakanso tsiku lotsatira osalekeza. Amene anagwira zokwana mahomeri* 10+ ndiwo amene anagwira zochepa. Ndipo anali kuziyanika paliponse, moti zinangoti mbwee, pamsasa wonsewo. 33 Nyamayo ikadali m’kamwa mwawo,+ asanaitafune, mkwiyo wa Yehova unawayakira+ anthuwo. Ndipo Yehova anayamba kuwakantha anthuwo n’kuwapha ambiri.+
34 Malo amenewo anawatcha Kibiroti-hatava,+ chifukwa anafotserapo anthu amene anasonyeza mtima wadyera.+ 35 Anthuwo atachoka pa Kibiroti-hatava, anasamukira ku Hazeroti,+ ndipo anakhala kumeneko.
12 Tsopano Miriamu ndi Aroni anayamba kum’nena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene anam’kwatira.+ 2 Iwo ankanena kuti: “Kodi Yehova walankhula kudzera kwa Mose yekha? Kodi sanalankhulenso kudzera kwa ife?”+ Koma Yehova anali kumvetsera.+ 3 Moseyo anali munthu wofatsa kwambiri+ kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.
4 Kenako Yehova anauza Mose, Aroni ndi Miriamu kuti: “Nonse atatu nyamukani, mupite kuchihema chokumanako.” Pamenepo atatuwo ananyamuka n’kupita. 5 Tsopano Yehova anatsika mumtambo woima njo ngati chipilala+ n’kuima pakhomo la chihema chokumanako, ndipo anaitana Aroni ndi Miriamu. Pamenepo iwo anayandikira kumeneko. 6 Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine m’masomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye m’maloto.+ 7 Koma sindikutero ndi mtumiki wanga Mose.+ Iye ndamuikiza nyumba yanga yonse.+ 8 Ndimalankhula naye pamasom’pamaso,+ kumuuza zinthu momveka bwino osati mophiphiritsa,+ ndipo amaona maonekedwe a Yehova.+ Tsopano n’chifukwa chiyani inu simunaope kum’nena Mose mtumiki wanga?”+
9 Pamenepo Yehova anawakwiyira koopsa, n’kuchokapo. 10 Kenako mtambo uja unachoka pamwamba pa chihemacho. Pomwepo, Miriamu anagwidwa ndi khate loyera mbuu!+ Aroni atacheuka, anangoona kuti Miriamu wachita khate.+ 11 Atangoona choncho, Aroni anachonderera Mose kuti: “Pepani mbuyanga, chonde, musawerengere tchimo limene tachita mopusali.+ 12 Chonde, musangomulekerera Miriamu kuti akhale ngati mwana wobadwa wakufa,+ wotuluka m’mimba mwa amayi ake mnofu wake utawola mbali ina.” 13 Pamenepo Mose anayamba kufuulira Yehova kuti: “Chonde Mulungu wanga! M’chiritseni chonde!”+
14 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanam’lavulira+ malovu kumaso, sakanakhala wonyazitsidwa masiku 7? Choncho m’tulutseni+ akakhale kunja kwa msasa masiku 7,+ pambuyo pake mum’landire mumsasamo.”+ 15 Chotero Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke kufikira Miriamu atalandiridwanso mumsasa. 16 Pambuyo pake, anthuwo anachoka ku Hazeroti,+ n’kukamanga msasa m’chipululu cha Parana.+
13 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 2 “Utume amuna kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+ Pa fuko lililonse utume mwamuna mmodzi, amene ali mtsogoleri+ wa fukolo.”
3 Chotero Mose anatumiza amunawo kuchokera kuchipululu cha Parana,+ monga mmene Yehova analamulira. Amuna onsewo anali atsogoleri a ana a Isiraeli. 4 Mayina awo ndi awa: Wa fuko la Rubeni anali Samuwa, mwana wa Zakuri. 5 Wa fuko la Simiyoni anali Safati, mwana wa Hori. 6 Wa fuko la Yuda anali Kalebe,+ mwana wa Yefune. 7 Wa fuko la Isakara anali Igali, mwana wa Yosefe. 8 Wa fuko la Efuraimu anali Hoshiya,+ mwana wa Nuni. 9 Wa fuko la Benjamini anali Paliti, mwana wa Rafu. 10 Wa fuko la Zebuloni anali Gadiyeli, mwana wa Sodi. 11 Wa fuko la Yosefe,+ loimira fuko la Manase,+ anali Gadidi mwana wa Susi. 12 Wa fuko la Dani anali Amiyeli, mwana wa Gemali. 13 Wa fuko la Aseri anali Seturi, mwana wa Mikayeli. 14 Wa fuko la Nafitali anali Nabi, mwana wa Vopisi. 15 Wa fuko la Gadi anali Geyuweli, mwana wa Maki. 16 Amenewa ndiwo mayina a amuna amene Mose anawatuma kuti akazonde dzikolo. Mose anatcha Hoshiya mwana wa Nuni kuti Yehoswa.*+
17 Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Pitani ku Negebu,+ ndipo mukafike kudera lamapiri.+ 18 Mukaone kuti dzikolo n’lotani.+ Mukaonenso ngati anthu a m’dzikomo ali amphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ali owerengeka kapena ambiri. 19 Mukaone ngati dziko limene akukhalamo lili labwino kapena loipa, ndiponso ngati akukhala m’misasa kapena m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. 20 Komanso mukaone ngati dzikolo lili lachonde kapena lopanda chonde,+ ngati lili ndi mitengo kapena ayi. Mukalimbe mtima+ n’kutengako zipatso za m’dzikomo.” Amenewa anali masiku amene mphesa zoyamba zinali kupsa.+
21 Choncho amunawo anapita kukazonda dzikolo, kuyambira kuchipululu cha Zini+ mpaka ku Rehobu,+ kufupi ndi Hamati.+ 22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe. 23 Atafika kuchigwa* cha Esikolo,+ anadula nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa,+ ndipo anthu awiri analinyamula paphewa ndi mitengo yonyamulira. Anatengakonso makangaza*+ ndi nkhuyu. 24 Malowo anawatcha chigwa cha Esikolo,+ chifukwa chakuti ana a Isiraeliwo anadulapo tsango la mphesa.
25 Potsirizira pake anabwerako kokazonda dziko kuja patatha masiku 40.+ 26 Iwo anabwera kwa Mose ndi Aroni, ndiponso kwa khamu lonse la ana a Isiraeli m’chipululu cha Parana, ku Kadesi.+ Anafotokozera onsewo za ulendo wawo n’kuwaonetsa zipatso za kudzikolo. 27 Anauza Mose kuti: “Tinakalowa m’dziko limene munatitumako. Ndithudi ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ndipo zipatso zake ndi izi.+ 28 Ngakhale zili choncho, anthu okhala kumeneko ndi anthu amphamvu zawo, mizinda yawo ndi yotchingidwa ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso yaitali.+ Si zokhazo, mbadwa za Anaki zija tinaziona kumeneko.+ 29 Aamaleki+ amakhala ku Negebu.+ Ahiti, Ayebusi+ ndi Aamori+ amakhala kudera lamapiri. Akanani+ amakhala m’mphepete mwa nyanja, ndi m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano.”
30 Pamenepo Kalebe+ anayesa kukhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, kenako anati: “Tiyeni tipite tsopano lino, tikalanda dzikolo, pakuti tikaligonjetsa ndithu.”+ 31 Koma amuna amene anapita naye limodzi ananena kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.”+ 32 Ndipo iwo anapitiriza kuuza ana a Isiraeliwo zoipa+ za dziko limene anakalizondalo, kuti: “Dziko limene tinakalizondalo limameza anthu ake, ndipo anthu onse amene tinawaona kumeneko ndi ziphona zamatupi akuluakulu.+ 33 Tinaonakonso Anefili,* mbadwa za Anaki,+ moti eni akefe tinangodziona ngati tiziwala kwa iwo. Iwonso ndi mmene anationera.”+
14 Pamenepo khamu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anachezera kulira+ usiku wonse. 2 Ana onse a Isiraeli anayamba kudandaula za Mose ndi Aroni.+ Ndipo khamu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera m’chipululu muno. 3 N’chifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+ 4 Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+
5 Mose ndi Aroni atamva zimenezi, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ pamaso pa khamu lonse la ana a Isiraeli. 6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni,+ ndi Kalebe mwana wa Yefune,+ amene anakazonda nawo dzikolo, anang’amba zovala zawo.+ 7 Iwo anauza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti: “Dziko limene tinakalowamo n’kulizonda, n’labwino kwambiri.+ 8 Yehova akatikomera mtima,+ ndithu adzatilowetsa m’dzikolo n’kulipereka kwa ife, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 9 Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+
10 Koma khamu lonselo linayamba kunena zoti liwaponye miyala.+ Kenako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa ana a Isiraeli onse pamwamba pa chihema chokumanako.+
11 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza kufikira liti?+ Kodi adzayamba liti kundikhulupirira pambuyo pa zizindikiro zonse zimene ndachita pakati pawo?+ 12 Ndiwagwetsera mliri ndi kuwafafaniza, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwowa.”+
13 Koma Mose anamuyankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene munalanditsako anthuwa mwa mphamvu zanu, adzamva ndithu zimenezi.+ 14 Iwo akamva adzauza anthu a m’dziko lino, amene amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ ndi kuti mumaonekera kwa iwo pamasom’pamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera mumtambo woima njo ngati chipilala, pamene usiku mumawatsogolera m’lawi lamoto.+ 15 Mukapha anthuwa kamodzi n’kamodzi ngati mukupha munthu mmodzi,+ ndithu mitundu imene yamva za ukulu wanu idzati, 16 ‘Chifukwa Yehova analephera kufikitsa anthuwo kudziko limene anawalumbirira, anangowaphera m’chipululu.’+ 17 Chonde Yehova, tsopano sonyezani ukulu wa mphamvu zanu,+ monga munanenera kuti, 18 ‘Yehova ndi wosakwiya msanga,+ ndipo ndi wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Amakhululukira wolakwa ndi wophwanya malamulo,+ koma iye salekerera konse wolakwa osam’langa.+ Amalanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za makolo awo.’+ 19 Chonde, khululukani kulakwa kwa anthuwa mwa kukoma mtima kwanu kosatha, ngati mmene mwakhala mukuwakhululukira kuchokera ku Iguputo mpaka pano.”+
20 Ndiyeno Yehova anati: “Chabwino, ndakhululuka chifukwa cha mawu ako.+ 21 Komanso, pali ine Mulungu wamoyo, dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi ulemerero wa Yehova.+ 22 Koma anthu onse amene aona ulemerero wanga,+ ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, ndi zimene ndachita m’chipululu, amene akupitirizabe kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, amenenso sanamvere mawu anga,+ 23 sadzaliona m’pang’ono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+ 24 Koma mtumiki wanga Kalebe,+ chifukwa wasonyeza kuti ali ndi mzimu wosiyana ndi wa ena, ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse,+ ndithudi ndidzam’lowetsa m’dziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzakhalamo ngati dziko lawo.+ 25 Popeza kuti Aamaleki ndi Akanani+ akukhala kuchigwa, mawa mutembenuke, munyamuke ulendo wolowera kuchipululu podzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.”+
26 Yehova anapitiriza kulankhula kwa Mose ndi Aroni, kuti: 27 “Kodi khamu la anthu oipa amenewa lidandaula motsutsana nane kufikira liti?+ Ndamva kudandaula konseko kumene ana a Isiraeli akuchita motsutsana nane.+ 28 Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, mudzandifunse ngati sindidzachita kwa inu monga mwa zimene mwakhala mukulankhula, zimene ndadzimvera ndekha m’makutu mwangamu.+ 29 Mitembo yanu idzagona m’chipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30 Inu simudzalowa m’dziko limene ndinachita kukweza dzanja langa+ polumbira kuti ndidzakhala nanu mmenemo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
31 “‘“Komanso, ana anu amene munati adzatengedwa ndi adani,+ nawonso ndidzawalowetsa m’dzikolo ndithu. Moti dziko limene inuyo mwalikana, iwo adzalidziwa bwino.+ 32 Koma inuyo mitembo yanu idzagona m’chipululu muno.+ 33 Ana anu adzakhala abusa m’chipululu+ kwa zaka 40, ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika*+ kwanu, mpaka womalizira kufa wa inu atagona m’manda m’chipululu.+ 34 Mwa kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, masiku 40,+ mudzalangidwanso kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi,+ kuti mudziwe kuipa kondipandukira.+
35 “‘“Ine Yehova ndalankhula, mudzandifunse ngati sindidzawafafaniza m’chipululu mommuno anthu oipa onsewa,+ amene agwirizana kuti atsutsane ndi ine. Onse adzathera m’chipululu mommuno.+ 36 Komanso amuna amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo, amene atabwerako anapangitsa anthu onse kudandaula motsutsana ndi Mose, mwa kunena zoipa zokhudza dzikolo,+ 37 amuna amene anadzanena zoipa zokhazokha zokhudza dzikolo, adzafa ndi mliri wa Yehova.+ 38 Koma mwa amuna amene anakazonda dzikolo, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, adzakhalabe ndi moyo ndithu.”’”+
39 Mose atalankhula mawuwo kwa ana onse a Isiraeli, anthu onsewo anayamba kulira kwambiri.+ 40 Komanso, iwo anadzuka m’mawa kwambiri kuti apite kudera lamapiri lija, ndipo anati: “Tiyeni! Ife tipita kumalo amene Yehova ananena, chifukwa tachimwa.”+ 41 Koma Mose anati: “N’chifukwa chiyani mukuphwanya lamulo la Yehova?+ Zimenezo sizikuthandizani. 42 Musapite kumeneko chifukwa Yehova sali nanu. Adani anuwo akakugonjetsani.+ 43 Kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanani,+ ndithu akakuphani ndi lupanga. Chifukwa mwasiya kutsatira Yehova, Yehovayo sapita nanu kumeneko.”+
44 Komabe, anthuwo ananyamuka mwa iwo okha ulendo wopita kudera lamapiri kuja,+ koma likasa la pangano la Yehova silinachoke pakati pa msasa. Mose nayenso sanachoke.+ 45 Koma Aamaleki+ ndi Akanani omwe anali kukhala kudera lamapirilo anatsika n’kuyamba kuwapha ndi kuwabalalitsa mpaka ku Horima.+
15 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Mukakafika m’dziko limene ndikukupatsani, kumalo amene muzikakhala,+ 3 popereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova,+ kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe yochitira lonjezo lapadera, kapena nsembe yongopereka mwaufulu,+ kapena yopereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti mufukize fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova+ la nyama ya ng’ombe kapena ya nkhosa, 4 wopereka nsembeyo, azikaperekanso kwa Yehova nsembe yambewu ya ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.* 5 Ndipo muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa.+ Azikakhala wokwanira gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini. Vinyoyo muzikam’pereka limodzi ndi nsembe yopsereza, kapena ndi nsembe ya mwana wa nkhosa wamphongo. 6 Komanso popereka nsembe ya nkhosa yamphongo, muzikaipereka limodzi ndi nsembe yambewu yokwanira magawo awiri a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. 7 Ndiponso muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini, monga fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.
8 “‘Koma ngati mukupereka ng’ombe yamphongo monga nsembe yopsereza,+ kapena monga nsembe yochitira lonjezo lapadera,+ kapenanso monga nsembe zachiyanjano kwa Yehova,+ 9 woperekayo azikapereka ng’ombe yamphongoyo limodzi ndi nsembe yambewu.+ Nsembe yambewuyo izikakhala yokwanira magawo atatu a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo azikauthira mafuta okwanira hafu ya muyezo wa hini. 10 Ndiponso muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa.+ Vinyoyo azikakhala wokwanira hafu ya muyezo wa hini. Akakhale nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 11 Izi n’zimene muyenera kuchita popereka ng’ombe yamphongo iliyonse, nkhosa yamphongo iliyonse, mwana wa nkhosa wamphongo, kapena mbuzi. 12 Muyenera kuchita zimenezi panyama iliyonse yoti mupereke nsembe, ngakhale zitachuluka motani. 13 Mbadwa iliyonse izichita zimenezi popereka nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
14 “‘Ngati mlendo wokhala pakati panu, kapena mlendo amene wakhala nanu kwa mibadwomibadwo, afunikira kupereka nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova, monga mmene inuyo muzichitira, iyenso azichita momwemo.+ 15 Inu amene mwapanga mpingo limodzi ndi alendo amene akukhala pakati panu, mukhale ndi malamulo amodzi.+ Amenewa ndiwo malamulo amene inuyo muziwatsatira mpaka kalekale m’mibadwo yanu. Mlendo azikhala chimodzimodzi ndi inu pamaso pa Yehova.+ 16 Pakhale malamulo ndi zigamulo zofanana kwa inu ndi kwa alendo amene akukhala nanu.’”+
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 18 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Mukakalowa m’dziko limene ndikukutengeraniko,+ 19 muzikapereka chopereka kwa Yehova pachakudya chilichonse cha m’dzikolo,+ chimene muzikadya. 20 Muzikapereka mikate yozungulira yoboola pakati ya ufa wamisere monga chopereka cha zipatso zoyambirira kucha.+ Muzikaipereka ngati mmene mumaperekera chopereka chochokera popunthira mbewu. 21 Muzipereka kwa Yehova ufa wamisere wa zipatso zanu zoyambirira ku mibadwo yanu yonse.
22 “‘Koma ngati mwachita cholakwa cholephera kusunga malamulo onsewa+ amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23 zonse zimene Yehova wakulamulirani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka ku mibadwo yanu yonse, 24 ngati khamulo lachita cholakwacho mosazindikira, pamenepo khamu lonselo lipereke ng’ombe yaing’ono yamphongo monga nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Apereke nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa monga mwa dongosolo la nthawi zonse.+ Aperekenso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ 25 Pamenepo wansembe azipereka nsembe yophimba machimo+ a khamu lonse la ana a Isiraeli. Akatero, anthuwo azikhululukidwa cholakwacho chifukwa anachita mosazindikira,+ komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova, ndiponso nsembe yamachimo kwa Yehova pa cholakwa chawocho. 26 Khamu lonse la ana a Isiraeli lizikhululukidwa+ limodzi ndi alendo amene akukhala pakati pawo, chifukwa anthu onsewo anachimwa mosazindikira.
27 “‘Ngati munthu angachimwe mosazindikira,+ apereke mbuzi yaikazi yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ 28 Wansembe apereke nsembe yophimba tchimo la munthuyo, amene walakwira Yehova mosazindikira, kuti akhululukidwe.+ 29 Munthu akachita tchimo mosazindikira, pazikhala lamulo limodzi, kwa mbadwa ya ana a Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.+
30 “‘Koma munthu amene wachita cholakwa mwadala,+ kaya akhale mbadwa kapena mlendo, kumene kuli kunyoza Yehova,+ munthuyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake.+ 31 Munthu ameneyo wanyoza mawu a Yehova,+ ndipo waphwanya malamulo ake.+ Aziphedwa ndithu mosalephera.+ Mlandu wa cholakwa chake uzikhala ndi iye mwini.’”+
32 M’chipululumo, tsiku lina ana a Isiraeli anapeza munthu wina akutola nkhuni pa tsiku la sabata.+ 33 Amene anam’peza akutola nkhuniwo anam’tengera kwa Mose ndi Aroni ndi kwa khamu lonselo. 34 Iwo anam’sunga kaye+ chifukwa panalibe lamulo lachindunji lonena chilango chimene akanapereka.
35 Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: “Munthuyo aphedwe basi!+ Khamu lonselo likam’ponye miyala kunja kwa msasa.”+ 36 Choncho khamu lonselo linam’tengera kunja kwa msasa kumene linakam’ponya miyala mpaka kufa, monga mmene Yehova analamulira Mose.
37 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 38 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti azisokerera mphonje m’mphepete mwa zovala zawo, ku mibadwo yawo yonse. Azisokereranso chingwe cha buluu pamwamba pa mphonje za zovalazo.+ 39 ‘Chingwecho chikhale ngati mphonje kwa inu, kuti mukachiyang’ana muzikumbukira malamulo onse+ a Yehova ndi kuwasunga. Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu,+ chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.+ 40 Ndakupatsani lamulo limeneli kuti muzikumbukira ndi kusunga malamulo anga onse, ndi kukhaladi oyera kwa Mulungu wanu.+ 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo, kuti ndionetse kuti ndine Mulungu wanu.+ Ndine Yehova Mulungu wanu.’”+
16 Tsopano Kora+ mwana wa Izara,+ mwana wa Kohati,+ mwana wa Levi,+ anagwirizana ndi adzukulu a Rubeni,+ omwe ndi Datani+ ndi Abiramu+ ana a Eliyabu,+ komanso Oni mwana wa Pelete, kuti aukire. 2 Iwo anaukira Mose. Oukirawo anali limodzi ndi amuna achiisiraeli okwanira 250. Iwowa anali atsogoleri a anthuwo, owaimira kumisonkhano, amuna otchuka. 3 Choncho iwo anasonkhana n’kuyamba kutsutsana+ ndi Mose ndi Aroni, kuti: “Tatopa nanu tsopano! Khamu lonseli ndi loyera,+ ndipo Yehova ali pakati pawo.+ Nanga n’chifukwa chiyani inu mukudzikweza pa mpingo wa Yehova?”+
4 Mose atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 5 Ndiyeno Mose analankhula ndi Kora ndiponso khamu lonselo, kuti: “Mawa m’mawa, Yehova aonetsa amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera.+ Aonetsa amene ayenera kuima pamaso pake,+ ndipo amene ati am’sankheyo+ adzaima pamaso pake. 6 Mudzachite izi: Iwe Kora ndi khamu lonselo,+ mudzatenge zofukizira.+ 7 M’zofukizirazo mudzaikemo moto ndiponso zofukiza ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova mawa. Munthu amene Yehova ati adzamusankhe,+ ameneyo ndiye woyera. Inenso ndatopa nanu, inu ana a Levi!”+
8 Ndipo Mose anapitiriza kulankhula ndi Kora, kuti: “Tamverani, inu ana a Levi. 9 Kodi amuna inu mukuyesa n’chinthu chaching’ono kuti Mulungu wa Isiraeli anakupatulani+ pakati pa Aisiraeli, n’kukutengani kukhala akeake, kuti muzitumikira Yehova pachihema chake ndi kutumikira khamulo?+ 10 Kodi ndi chinthu chaching’ono kuti Mulungu anakuyandikizani kwa iye, limodzi ndi abale anu onse, ana a Levi? Kodi tsopano anthu inu mukufunanso udindo waunsembe?+ 11 Zimene mukuchitazi, iweyo limodzi ndi khamu lako lonseli, mukuukira Yehova.+ Kunena za Aroni, kodi iye ndani kuti amuna inu mum’dandaule?”+
12 Pambuyo pake, Mose anatuma mthenga kukaitana Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu. Koma iwo anayankha kuti: “Ife sitibwerako kumeneko!+ 13 Kodi ukuyesa n’chinthu chaching’ono kuti unatichotsa kudziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphere m’chipululu muno,+ kutinso ukhale ngati mfumu yomatilamula?+ 14 Si izi nanga, sunatifikitse kudziko lililonse loyenda mkaka ndi uchi,+ kumene ungatigawire malo ndiponso minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuti amunawo uwakolowole maso? Tatitu kumeneko sitibwerako!”
15 Mose atamva zimenezi anakwiya kwambiri, ndipo anauza Yehova kuti: “Nsembe zawo zambewu musaziyang’ane.+ Ine sindinawalande ngakhale bulu mmodzi wamphongo, kapena kuchitira choipa aliyense wa iwo.”+
16 Kenako Mose anauza Kora+ kuti: “Mawa, iweyo ndi khamu lako lonse mukaonekere pamaso pa Yehova.+ Mukaonekere, iweyo limodzi ndi khamulo, ndi Aroni. 17 Aliyense akatenge chofukizira chake. Mukaikemo nsembe yofukiza, ndipo aliyense adzabweretse chofukizira chake pamaso pa Yehova. Zofukizirazo zidzakhalepo zokwanira 250, komanso iweyo ndi Aroni aliyense adzakhale ndi chake.” 18 Choncho aliyense wa iwo anatenga chofukizira chake n’kuikamo moto ndi nsembe yofukiza. Atatero, anakaimirira pakhomo la chihema chokumanako limodzi ndi Mose ndi Aroni. 19 Kora atasonkhanitsa khamu+ lonse lotsutsana nawo pakhomo la chihema chokumanako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa khamu lonselo.+
20 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndiponso Aroni, kuti: 21 “Chokani+ pakati pa khamu ili, kuti ndiwafafanize+ kamodzi n’kamodzi.” 22 Anthuwo atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, n’kunena kuti: “Chonde Mulungu, inu Mulungu amene amapereka moyo kwa zamoyo zonse,+ kodi kuchimwa kwa munthu mmodzi yekha n’kumene mungapsere mtima khamu lonseli?”+
23 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 24 “Uza khamulo kuti, ‘Chokani kumahema a Kora, Datani ndi Abiramu!’”+
25 Kenako Mose ananyamuka n’kupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu+ a Isiraeli anapita naye limodzi. 26 Atafika anauza khamulo kuti: “Chonde, chokani kumahema a anthu oipawa, ndipo musakhudze chinthu chawo chilichonse,+ kuti musaphedwe nawo limodzi chifukwa cha kuchimwa kwawo.” 27 Nthawi yomweyo anthuwo anachoka kumbali zonse za mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Zitatero, Datani ndi Abiramu anatuluka n’kuima pamakomo a mahema awo,+ limodzi ndi akazi awo, ana awo.
28 Ndiyeno Mose anati: “Mudziwira izi kuti Yehova ndiye anandituma kuti ndichite zonsezi,+ ndiponso kuti si za mumtima mwanga ayi:+ 29 Ngati anthuwa angafe mmene anthu onse amafera, ndipo ngati angalangidwe ndi chilango cha anthu,+ pamenepo, ndiye kuti sindinatumidwe ndi Yehova.+ 30 Koma ngati angafe ndi chinthu chachilendo chimene Yehova achite,+ kuti nthaka iyasame n’kuwameza iwo+ ndi zonse ali nazo, moti iwo n’kutsikira ku Manda*+ ali amoyo, pamenepo mudziwa ndithu kuti amunawa anyoza+ Yehova.”
31 Mose atangomaliza kulankhula mawu amenewa, nthaka imene iwo anapondapo inayamba kung’ambika.+ 32 Nthakayo inatsegula pakamwa pake n’kuwameza iwowo ndi mabanja awo, limodzi ndi anthu ena onse amene anali kumbali ya Kora, komanso katundu wawo yense.+ 33 Chotero iwo analowa m’nthaka, limodzi ndi onse amene anali kumbali yawo. Iwo anatsikira ku Manda ali amoyo. Nthakayo inawafotsera,+ moti iwo anafafanizika pakati pa mpingo wonse.+ 34 Pamenepo, Aisiraeli onse amene anali pamalopo anayamba kuthawa atamva kufuula kwawo, ndipo anati: “Tikuopa kuti nthaka ingatimeze nafenso!”+ 35 Ndiyeno panabuka moto wochokera kwa Yehova,+ umene unapsereza amuna 250 omwe anali kupereka nsembe zofukiza+ aja.
36 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 37 “Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse zofukizira+ pamotowo, ‘Ndipo umwaze makalawo. Zofukizirazo n’zopatulika, 38 zofukizira za amuna amene anafa+ chifukwa cha kuchimwa. Azisule kuti zikhale timalata topyapyala n’kukutira nato guwa lansembe,+ popeza anafika nazo pamaso pa Yehova, ndipo zakhala zopatulika. Timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli.’”+ 39 Chotero, wansembe Eleazara anatenga zofukizira+ zamkuwa zimene anabwera nazo anthu amene anapsa ndi moto aja, ndipo anazisula n’kuzipanga timalata tokutira guwa lansembe. 40 Eleazara anachita izi kuti timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli, kuti munthu aliyense amene si mbadwa+ ya Aroni asayandikire kwa Yehova+ kukafukiza nsembe. Anateronso kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi gulu lake+ anachita. Eleazara anachita zonse monga mmene Yehova anamuuzira kudzera kwa Mose.
41 Koma tsiku lotsatira, khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose ndi Aroni,+ kuti: “Mwapha anthu a Yehova inu.” 42 Khamulo litasonkhana pamodzi kuti liukire Mose ndi Aroni, linacheukira kuchihema chokumanako. Anthuwo anangoona kuti mtambo waphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova wayamba kuonekera.+
43 Tsopano Mose ndi Aroni anakaima patsogolo pa chihema chokumanako.+ 44 Pamenepo Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 45 “Amuna inu, chokani pakati pa khamuli kuti ndilifafanize kamodzi n’kamodzi.”+ Atamva zimenezi, iwo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 46 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Tenga chofukizira uikemo moto wochokera paguwa lansembe.+ Uikemo nsembe yofukiza n’kupita kwa khamulo mofulumira kuti ukawaphimbire machimo awo.+ Chita zimenezi chifukwa Yehova wakwiya kwambiri.+ Mliritu wayamba kale!” 47 Nthawi yomweyo Aroni anatenga chofukiziracho monga anamuuzira Mose, n’kuthamanga kukalowa pakati pa mpingowo. Koma mliri unali utayamba kale pakati pawo. Choncho Aroni anaika nsembe ija pamoto n’kuyamba kuwaphimbira machimo anthuwo. 48 Aroni anaimabe chilili pakati pa akufa ndi amoyo.+ Kenako mliriwo unaleka.+ 49 Amene anaphedwa ndi mliriwo anakwana 14,700, kupatula amene anaphedwa chifukwa cha Kora aja. 50 Pamapeto pake, pamene Aroni anabwerera kwa Mose pakhomo la chihema chokumanako, mliriwo unali utaleka.
17 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo utenge ndodo+ ya fuko lililonse kwa mtsogoleri+ wa fukolo. Zikhalepo ndodo 12. Pandodo iliyonse ulembepo dzina la mtsogoleri wa fukolo. 3 Pandodo ya fuko la Levi ulembepo dzina la Aroni. Pakuti mtsogoleri aliyense ali ndi ndodo ya fuko lawo. 4 Ndodozo uziike m’chihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+ 5 Chimene chichitike n’chakuti, munthu amene ndimusankheyo,+ ndodo yake idzaphuka, ndipo ndidzathetseratu kudandaula+ kwa ana a Isiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine, pamene akudandaula motsutsana nawe.”+
6 Choncho, Mose analankhula ndi ana a Isiraeli. Aliyense wa atsogoleri awo anapereka ndodo+ yake, malinga ndi fuko lawo. Zinalipo ndodo 12, ndipo imodzi ya ndodozo+ inali ya Aroni. 7 Ndiyeno Mose anakaika ndodozo pamaso pa Yehova m’chihema cha Umboni.+
8 Tsiku lotsatira, Mose atalowa m’chihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni ya nyumba ya Levi inali itaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inali kumasula maluwa ndi kubala zipatso za amondi zakupsa. 9 Tsopano Mose anachotsa ndodo zonse pamaso pa Yehova n’kupita nazo kwa ana a Isiraeli onse. Amuna aja anayang’ana ndodozo, ndipo aliyense anatengapo yake.
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo+ ya Aroni patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana a chipandukowa,+ n’cholinga chakuti aleke kudandaula motsutsana ndi ine, kuti angafe.” 11 Nthawi yomweyo, Mose anachita monga momwe Yehova anamulamulira. Anachitadi momwemo.
12 Tsopano ana a Isiraeli anayamba kuuza Mose kuti: “Tsopano ife tifa ndithu! Ndithudi titha ife! Tonse titha basi.+ 13 Aliyense amene ayandikire+ chihema cha Yehova, afa!+ Koma zoona ife tithe mwa njira imeneyi?”+
18 Tsopano Yehova analankhula ndi Aroni kuti: “Iwe ndi ana ako, ndi nyumba yonse ya bambo ako, mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza malo opatulika.+ Iweyo ndi ana ako mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza unsembe wanu.+ 2 Utengenso abale ako a fuko la Levi, amtundu wa bambo ako, kuti azikhala pafupi ndi inu. Azitumikira+ iweyo limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+ 3 Azitumikira inuyo ndi kugwira ntchito zawo za pachihema chonse.+ Koma asamayandikire zipangizo za m’malo oyera, kapena kuyandikira guwa lansembe kuti iwowo kapena inuyo mungafe.+ 4 Azikhala pafupi nanu kuti azichita utumiki wawo wonse wa pachihema chokumanako, ndipo munthu wina aliyense amene si Mlevi asayandikire kwa inu.+ 5 Muzichita utumiki wanu m’malo oyera+ ndi paguwa lansembe,+ kuti mkwiyo+ usadzawabukirenso ana a Isiraeli. 6 Inetu ndatenga abale anu Alevi, mwa ana a Isiraeli,+ ndipo ndawapereka kwa inu monga mphatso yanu.+ Iwowa akhala operekedwa kwa Yehova kuti atumikire pachihema chokumanako.+ 7 Iweyo ndi ana ako, muzichita utumiki wanu waunsembe mosamala pa chilichonse chokhudza guwa lansembe, ndiponso pa zonse zamkati, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Umenewu ndiwo utumiki wanu.+ Unsembewu ndikukupatsani monga mphatso, ndipo aliyense wosakhala Mlevi akayandikira pafupi aziphedwa.”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni, kuti: “Inetu ndakupatsa udindo woyang’anira zopereka zonse zoperekedwa kwa ine.+ Pa zinthu zonse zopatulika zimene ana a Isiraeli azipereka, ndakupatsako gawo iweyo ndi ana ako, likhale gawo lanu mpaka kalekale.+ 9 Gawo limenelo lizikhala lako pazopereka zopatulika koposa, ndizo nsembe zonse zotentha ndi moto. Nsembezo, zimene azibwera nazo kwa ine, ndi izi: Nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo,+ nsembe zawo za kupalamula,+ ndi nsembe zawo zina zonse. Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako. 10 Uzilidyera m’malo oyera koposa,+ ndipo mwamuna aliyense azidyako.+ Gawo limenelo lizikhala chinthu chopatulika kwa iwe.+ 11 Mphatso zonse za ana a Isiraeli, limodzi ndi nsembe zawo zonse zoweyula*+ zimene azipereka monga zopereka zawo,+ zizikhala zako. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna, limodzi ndi ana ako aakazi.+ Zikhale gawo lanu mpaka kalekale. Aliyense wa m’nyumba yako amene ndi wosadetsedwa azidya nawo.+
12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+ 13 Zipatso zonse zoyamba kupsa m’minda yawo, zimene azizipereka kwa Yehova zizikhala zako.+ Aliyense wa m’nyumba yako amene ndi wosadetsedwa azidya nawo.
14 “Chinthu chilichonse chimene anthu apatulira Mulungu mu Isiraeli chizikhala chako.+
15 “Chamoyo chilichonse chotsegula mimba ya mayi ake,+ chimene chiziperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe, uzionetsetsa kuti ukuwombola mwana woyamba kubadwa wa munthu.+ Uziwombolanso+ mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa. 16 Mwanayo uzimuwombola ndi dipo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo. Uzimuwombola ndi mtengo woikidwiratu, masekeli asiliva asanu, malinga ndi sekeli la kumalo oyera,+ lofanana ndi magera+ 20. 17 Koma usawombole ng’ombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi+ ake uziwawaza paguwa lansembe, ndipo mafuta ake uziwafukiza pamoto monga nsembe yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 18 Uzitenga nyama yake kuti ikhale yako, mofanana ndi nganga ya nsembe yoweyula, komanso mwendo wam’mbuyo wakumanja.+ 19 Zopereka zonse zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova, ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, ngati gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano losatha* limene lidzakhala mpaka kalekale pakati pa Yehova ndi iwe ndi mbadwa zako.”+
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni, kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa m’dziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa gawo lililonse pakati pawo.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Isiraeli.+
21 “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako. 22 Ana a Isiraeli asadzayandikirenso chihema chokumanako, kuti angadzachimwe n’kufa.+ 23 Aleviwo azichita utumiki wawo pachihema chokumanako, ndipo ndiwo amene azisenza zolakwa za anthuwo.+ Iwo asakhale ndi cholowa+ pakati pa ana a Isiraeli. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale m’mibadwo yanu yonse. 24 Chakhumi chimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova monga chopereka, ndawapatsa Alevi monga cholowa chawo. N’chifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa ana a Isiraeli.’”+
25 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 26 “Lankhula ndi Alevi, uwauze kuti, ‘Muzilandira kwa ana a Isiraeli chakhumi chimene ndakupatsani monga cholowa+ chanu. Ndipo pachakhumi chimene muzilandiracho, muziperekapo chopereka chanu kwa Yehova, chakhumi cha chakhumicho.+ 27 Chakhumicho ndicho chizikhala chopereka chanu, monga cha tirigu wochokera pamalo popunthira,+ ndi cha vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa, kapena cha mafuta ochuluka ochokera m’chofinyira mafuta. 28 Mwa njira imeneyi, inunso muzipereka chopereka chanu kwa Yehova. Muzipereka kuchokera pazakhumi zonse zimene muzilandira kuchokera kwa ana a Isiraeli. Kuchokera pazakhumizo, muzipereka chopereka chanu kwa Yehova mwa kupatsa wansembe Aroni. 29 Pamphatso zonse zosiyanasiyana zoperekedwa kwa inu, inunso muziperekapo chopereka kwa Yehova. Muzipereka gawo lake labwino koposa,+ monga chinthu chopatulika chimene iwo apereka.’
30 “Ndipo uwauze kuti, ‘Mukapereka zabwino koposa za zoperekazo,+ zotsalazo zizikhala za Alevinu, monga tirigu wochokera popunthira, vinyo wochokera mopondera mphesa, kapena mafuta ochokera m’chofinyira mafuta. 31 Inuyo ndi a m’nyumba zanu muzidya zimenezo pamalo alionse, chifukwa ndizo malipiro anu pa utumiki umene muzichita m’chihema chokumanako.+ 32 Musachimwe polephera kupereka gawo labwino koposa la zinthuzo, ndipo musaipitse zinthu zopatulika za ana a Isiraeli, kuti mungafe.’”+
19 Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Nali lamulo limene Yehova wapereka. Iye wati, ‘Lankhulani ndi ana a Isiraeli kuti akupatseni ng’ombe yaikazi yofiira, yathanzi. Ng’ombeyo ikhale yopanda chilema+ yomwe sinamangidwepo m’goli chikhalire.+ 3 Mupereke ng’ombeyo kwa wansembe Eleazara kuti aitsogolere kunja kwa msasa, ndipo kumeneko ikaphedwe pamaso pake. 4 Kenako, wansembe Eleazara atengeko magazi a ng’ombeyo ndi chala chake, n’kuwawaza maulendo 7 moyang’anizana ndi chihema chokumanako.+ 5 Ndiyeno ng’ombeyo itenthedwe iyeyo akuona. Atenthe chikopa chake, nyama yake, magazi ake, limodzi ndi ndowe zake.+ 6 Wansembeyo atenge mtengo wa mkungudza,+ kamtengo ka hisope+ ndi ulusi wofiira kwambiri,+ aziponye pakati pa moto umene akutenthapo ng’ombeyo. 7 Akatha, wansembeyo achape zovala zake n’kusamba thupi lake ndi madzi. Pambuyo pake akhoza kulowa mumsasa, koma akhalebe wodetsedwa mpaka madzulo.
8 “‘Munthu amene atenthe ng’ombeyo achape zovala zake n’kusamba thupi lake ndi madzi,+ koma akhalebe wodetsedwa mpaka madzulo.
9 “‘Ndiyeno munthu wosadetsedwa awole phulusa+ la ng’ombeyo, akalithire pamalo oyera kunja kwa msasawo. Phulusalo alisunge kuti azilithira m’madzi oyeretsera+ khamu la ana a Isiraeli. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Wowola phulusa la ng’ombeyo azichapa zovala zake, koma azikhalabe wodetsedwa mpaka madzulo.+
“‘Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale kwa ana a Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.+ 11 Aliyense wokhudza mtembo wa munthu aliyense,+ nayenso azikhala wodetsedwa masiku 7.+ 12 Munthu woteroyo azidziyeretsa ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu,+ ndipo pa tsiku la 7 azikhala woyera. Koma akapanda kudziyeretsa pa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera pa tsiku la 7. 13 Munthu aliyense wokhudza mtembo, thupi la munthu aliyense amene angamwalire, amene sadzadziyeretsa, adzaipitsa chihema cha Yehova.+ Munthu ameneyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa Isiraeli.+ Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanawazidwe madzi oyeretsera.+ Chidetso chake chikadali pa iye.+
14 “‘Ngati munthu angafere muhema, nali lamulo lake: Munthu aliyense wolowa muhemamo, ndi aliyense amene ali mmenemo, akhale wodetsedwa masiku 7. 15 Chiwiya+ chilichonse chosavundikira bwino* chikhale chodetsedwa. 16 Aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu amene waphedwa ndi lupanga,+ kapena mtembo uliwonse, kapenanso fupa la munthu,+ ngakhalenso manda a munthu, akhale wodetsedwa masiku 7. 17 Munthu wodetsedwayo am’tapireko phulusa la nsembe yamachimo yotenthedwa ija. Phulusalo aliike m’mbiya n’kuthiramo madzi a kumtsinje. 18 Ndiyeno munthu wosadetsedwa+ atenge kamtengo ka hisope.+ Akaviike m’madziwo n’kuwaza hemalo. Awazenso ziwiya zonse ndi anthu onse amene anali muhemalo. Komanso, awaze munthu amene anakhudza fupa la munthu, kapena kukhudza munthu wophedwa, kapenanso mtembo uliwonse, ngakhalenso manda a munthu. 19 Munthu wosadetsedwayo awaze madziwo munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu, ndi pa tsiku la 7. Ndipo pa tsiku la 7+ limenelo amuyeretse tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake, asambe ndi madzi, ndipo akhale woyera madzulo ake.
20 “‘Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo aphedwe+ kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, chifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera. Choncho ndi wodetsedwa.
21 “‘Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale kwa iwo, kuti munthu wowaza madzi oyeretsera, komanso munthu amene angakhudze madziwo, azichapa zovala zake.+ Akatero, azikhalabe wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chinthu chilichonse chimene munthu wodetsedwayo angakhudze, chikhale chodetsedwa.+ Komanso munthu amene angakhudze chinthucho, akhale wodetsedwa mpaka madzulo.’”+
20 Tsopano khamu lonse la ana a Isiraeli linafika m’chipululu cha Zini,+ m’mwezi woyamba, ndipo anthuwo anakhala ku Kadesi.+ Kumeneko n’kumene Miriamu+ anafera n’kuikidwa m’manda.
2 Koma anthuwo anasowa madzi pamalopo, ndipo khamu+ lonselo linasonkhana n’kuukira Mose ndi Aroni.+ 3 Pamenepo anthuwo anayamba kukangana+ ndi Mose, kuti: “Zikanakhala bwino tikanangofera limodzi ndi abale athu amene anafa pamaso pa Yehova aja.+ 4 N’chifukwa chiyani anthu inu mwafikitsa mpingo wa Yehova kuchipululu chino, kuti ife limodzi ndi ziweto zathu tifere kuno?+ 5 N’chifukwa chiyani munatitulutsa m’dziko la Iguputo kutibweretsa kumalo oipa ano?+ Malo anji osamera mbewu iliyonse? Mitengo ya nkhuyu kulibe kuno, ngakhale mitengo ya mpesa, kapena mitengo ya makangaza.+ Ndi madzi akumwa omwe kulibe!” 6 Pamenepo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa mpingowo n’kupita kukhomo la chihema chokumanako. Kumeneko, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo ulemerero wa Yehova unayamba kuonekera kwa iwo.+
7 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 8 “Tenga ndodoyo,+ ndipo iwe ndi m’bale wako Aroni, musonkhanitse khamu lonse la anthuwo. Muuze thanthwe pamaso pawo kuti litulutse madzi. Utulutse madzi m’thanthweli kuti upatse khamulo, kuti limwe limodzi ndi ziweto zawo.”+
9 Choncho Mose anatenga ndodo ija pamaso pa Yehova,+ monga mmene anamulamulira. 10 Kenako, Mose ndi Aroni anasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi patsogolo pa thanthwelo, ndipo Mose anawauza kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu!+ Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?”+ 11 Mose atatero, anakweza dzanja lake n’kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake. Pamenepo madzi ambiri anayamba kutuluka, ndipo khamu lonselo linayamba kumwa madziwo limodzi ndi ziweto zawo.+
12 Pambuyo pake Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Chifukwa simunasonyeze chikhulupiriro mwa ine, polephera kundilemekeza+ pamaso pa ana a Isiraeli, simudzaulowetsa mpingowu m’dziko limene ndidzawapatse.”+ 13 Madzi amenewo anatchedwa madzi a ku Meriba,*+ chifukwa pamalopo ana a Isiraeli anakanganapo ndi Yehova, ndipo iye anakwezeka pakati pawo.
14 Tsiku lina Mose anatumiza amithenga kuchokera ku Kadesi kumene iwo anali, kupita kwa mfumu ya Edomu,+ kukanena kuti: “Abale anu Aisiraeli+ akuti, ‘Inu mukudziwa bwino za mavuto onse amene ationekera ife.+ 15 Paja kale makolo athu anapita ku Iguputo,+ ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri.+ Aiguputowo anatizunza ife ndi makolo athu.+ 16 Potsirizira pake, tinalirira Yehova.+ Iye anamva kulira kwathu, ndipo anatitumizira mngelo+ n’kutitulutsa m’dziko la Iguputo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m’malire a dziko lanu. 17 Chonde mutilole tidzere m’dziko lanu. Sitidzera m’munda wanu uliwonse, kapena m’munda wa mpesa uliwonse. Sitimwa madzi a pachitsime chanu chilichonse. Tizingoyenda+ mumsewu wa mfumu, osapatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ mpaka titadutsa m’dziko lanu.’”
18 Koma mfumu ya Edomu inawayankha kuti: “Musadzere m’dziko langa, chifukwa ndingatuluke ndi lupanga kudzakuthirani nkhondo.” 19 Ana a Isiraeliwo anayankha kuti: “Ife tidzangodutsa mumsewu waukulu, ndipo ngati tidzamwa madzi anu, ife kapena ziweto zathu, ndithu tidzalipira mtengo wake.+ Sitikufuna chilichonse ayi, koma kungodutsa m’dziko lanu basi.”+ 20 Koma iye anakanabe, kuti: “Ayi, musadzere+ m’dziko langa.” Mfumu ya Edomu+ itanena zimenezi, inatuluka ndi chikhamu cha anthu, ndi gulu la asilikali lamphamvu, kuti akawathire nkhondo. 21 Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera m’dziko lake.+ Motero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+
22 Kenako khamu lonse la ana a Isiraeli linanyamuka ku Kadesi+ kuja n’kukafika kuphiri la Hora.+ 23 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni m’phiri la Hora, m’malire a dziko la Edomu, kuti: 24 “Aroni aikidwe m’manda, agone ndi makolo ake,+ pakuti sadzalowa m’dziko limene ndidzapatse ana a Isiraeli. Izi zili choncho chifukwa amuna inu munapandukira malangizo anga okhudza madzi a ku Meriba.+ 25 Utenge Aroni ndi mwana wake Eleazara n’kukwera nawo phiri la Hora. 26 M’phirimo, ukamuvule Aroni zovala zake zaunsembe,+ n’kuveka mwana wake Eleazara.+ Aroni akamwalira kumeneko n’kugona ndi makolo ake.”+
27 Choncho Mose anachitadi zimene Yehova anamulamula. Pamaso pa khamu lonselo, iwo anakwera m’phiri la Hora. 28 Kumeneko, Mose anavula Aroni zovala zake zaunsembe n’kuveka mwana wake Eleazara. Pambuyo pake, Aroni anamwalira pamwamba pa phiripo.+ Potsirizira pake, Mose ndi Eleazara anatsika m’phirimo. 29 Tsopano khamu lonse la anthuwo litaona kuti Aroni wamwalira, nyumba yonse ya Isiraeli inalira maliro a Aroni masiku 30.+
21 Tsopano mfumu ya Akanani ya ku Aradi+ yomwe inali kukhala ku Negebu,+ inamva kuti Aisiraeli akubwera kudzera njira ya ku Atarimu. Itamva zimenezo inapita kukamenyana nawo ndipo Aisiraeli ena inawagwira ndi kupita nawo kudziko lake. 2 Aisiraeli ataona zimenezo, analonjeza kwa Yehova kuti:+ “Mukapereka anthuwa m’manja mwathu, ndithu ifenso tidzawononga mizinda yawo.”+ 3 Yehova anamva mawu a Aisiraeli, ndipo anapereka Akananiwo m’manja mwawo. Aisiraeli anawononga Akananiwo limodzi ndi mizinda yawo. N’chifukwa chake malowo anawatcha Horima.*+
4 Pamene Aisiraeliwo anali pa ulendo kuchokera kuphiri la Hora+ kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira, kulambalala dziko la Edomu,+ anayamba kutopa chifukwa cha njirayo. 5 Choncho iwo anayamba kuwiringula kwa Mulungu+ ndiponso Mose,+ kuti: “Munatitulutsiranji m’dziko la Iguputo? Kodi mumafuna kuti tidzafere m’chipululu?+ Kuno chakudya kulibe, madzinso kulibe.+ Chakudya chonyansachi chafika potikola.”+ 6 Pamenepo Yehova anatumiza njoka zapoizoni pakati pawo,+ ndipo zinayamba kuwaluma moti Aisiraeli ambiri anafa.+
7 Anthuwo ataona zimenezo, anapita kwa Mose n’kumuuza kuti: “Tachimwa ife,+ chifukwa talankhula mowiringula kwa Yehova ndiponso kwa inuyo. Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.”+ Pamenepo Mose anayamba kuwapepesera kwa Mulungu.+ 8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Upange chifanizo cha njoka yapoizoni* ndipo uchiike pamtengo wachizindikiro. Munthu aliyense amene walumidwa, akayang’ana njokayo akhalebe ndi moyo.”+ 9 Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa+ ndi kuiika pamtengo wachizindikirowo.+ Ndipo zinachitikadi kuti munthu akalumidwa ndi njoka n’kuyang’ana+ njoka yamkuwayo, anali kukhalabe ndi moyo.+
10 Pambuyo pake, ana a Isiraeli anasamuka n’kukamanga msasa ku Oboti.+ 11 Kenako anasamuka ku Oboti n’kukamanga msasa ku Iye-abarimu,+ m’chipululu choyang’anana ndi dziko la Mowabu, kotulukira dzuwa. 12 Atachoka kumeneko anakamanga msasa m’chigwa* cha Zeredi.+ 13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa m’dera la chigwa cha Arinoni,+ m’chipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori. 14 N’chifukwa chake buku la Nkhondo za Yehova limati:
“Vahebi ku Sufa, ndi zigwa* za Arinoni. 15 Mitsinje ya m’zigwazo imakafika ku Ari+ ndipo imayenda m’malire a dziko la Mowabu.”
16 Atachoka kumeneko anapita ku Beere.+ Kumeneku ndi kuchitsime kumene Yehova anauza Mose kuti: “Sonkhanitsa anthuwo kuti ndiwapatse madzi.”+
17 Pa nthawi imeneyo Aisiraeli anaimba nyimbo+ yakuti:
“Tumphuka, chitsime iwe! Vomerezani nyimboyo, anthu inu!
18 Chitsimechi n’chokumbidwa ndi akalonga. Chofukula anthu olemekezeka,
Chofukula ndi ndodo ya mtsogoleri wa asilikali,+ chofukula ndi ndodo zawo.”
Atachoka kuchipululucho anafika ku Matana. 19 Atachoka ku Matana anafika ku Nahaliyeli, ndipo atachoka ku Nahaliyeli anafika ku Bamoti.+ 20 Atachoka ku Bamoti anafika kuchigwa cha dziko la Mowabu,+ kumalire ndi mzinda wa Pisiga.+ Chitunda cha Pisiga chinayang’anana ndi dera la Yesimoni.+
21 Tsopano Aisiraeli anatuma amithenga kupita kwa Sihoni+ mfumu ya Aamori kukanena kuti: 22 “Tiloleni tidzere m’dziko lanu. Sitipatukira pamunda uliwonse, kapena pamunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mumsewu wa mfumu mpaka titadutsa m’dziko lanu.”+ 23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adzere m’dziko lake.+ M’malomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse n’kupita kukamenyana ndi Aisiraeli m’chipululumo. Anakafika ku Yahazi,+ kumene anayamba kumenyana ndi Aisiraeli. 24 Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ n’kuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi ana a Amoni, chifukwa Yazeri+ ali kumalire kwa ana a Amoni.+
25 Choncho Aisiraeli analanda mizinda yonseyi n’kuyamba kukhala m’mizinda yonse ya Aamori+ ku Hesiboni,+ ndi m’midzi yake yonse yozungulira. 26 Anayamba kukhala kumeneko chifukwa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni.+ Sihoni inali mfumu ya Aamori,+ ndipo iye ndiye anamenyana ndi mfumu ya Mowabu m’mbuyomo, n’kulanda dziko lonse limene linali m’manja mwake mpaka kuchigwa cha Arinoni.+ 27 N’chifukwa chake olakatula ndakatulo zonyoza anali kunena kuti:
“Bwerani ku Hesiboni.
Mzinda wa Sihoni umangidwe n’kukhala wolimba.
28 Pakuti moto watuluka ku Hesiboni,+ lawi lamoto latuluka m’tauni ya Sihoni.
Lanyeketsa Ari+ mzinda wa ku Mowabu, lanyeketsa eni ake a malo okwezeka a ku Arinoni.
29 Tsoka iwe Mowabu! Ndithu mudzafafanizika, inu anthu a Kemosi!+
Ndithudi, iye adzapangitsa ana ake aamuna kukhala othawa kwawo, ndipo adzapereka ana ake aakazi mu ukapolo kwa Sihoni, mfumu ya Aamori.
30 Choncho tiyeni tiwalase.
Ndithu Hesiboni adzafafanizika mpaka ku Diboni,+
Amayi adzaphedwa mpaka ku Nofa, amuna mpaka ku Medeba.”+
31 Tsopano Aisiraeli anayamba kukhala m’dziko la Aamori.+ 32 Pamenepo Mose anatumiza anthu ena kuti akazonde mzinda wa Yazeri.+ Atatero, Aisiraeliwo analanda midzi yozungulira mzindawo, n’kupitikitsa Aamori omwe anali kukhalamo.+ 33 Pambuyo pake, anatembenuka ndi kulowera njira ya ku Basana.+ Pamenepo, Ogi+ mfumu ya Basana inatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kukamenyana nawo pankhondo ya ku Edirei.+ 34 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndim’pereka ndithu m’manja mwako. Ndim’pereka pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake.+ Umuchite zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anali kukhala m’Hesiboni.”+ 35 Choncho Aisiraeliwo anapha iyeyo, ana ake ndi anthu ake onse, moti sipanatsale ndi mmodzi yemwe wopulumuka,+ ndipo analanda dziko lake.+
22 Kenako, ana a Isiraeli anasamuka kumaloko n’kukamanga msasa m’chipululu cha Mowabu,+ moyang’anana ndi Yeriko patsidya pa mtsinje wa Yorodano. 2 Tsopano Balaki+ mwana wa Zipori, anaona zonse zimene Aisiraeli anachita kwa Aamori. 3 Amowabu anachita mantha kwambiri ndi anthuwo chifukwa cha kuchuluka kwawo. Iwo anagwidwa mantha aakulu poopa ana a Isiraeliwo.+ 4 Pamenepo Amowabu anakalankhula ndi akuluakulu a ku Midiyani,+ kuti: “Chikhamuchi chidzamwetula malo athu onse monga ng’ombe yomwetula msipu kubusa.”
Pa nthawi imeneyo, Balaki+ mwana wa Zipori ndiye anali mfumu ya Mowabu. 5 Tsopano iye anatumiza amithenga kwa Balamu,+ mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje*+ wa m’dziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane, kuti: “Taonani! Anthu ochokera ku Iguputo afika kuno. Iwo adzaza dziko lino kulikonse kumene munthu angayang’ane,+ ndipo akukhala pafupi penipeni moyang’anana ndi ine. 6 Tsopano tabwerani chonde, mudzanditembererere+ anthuwa chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo, kuti mwina ndingawagonjetse n’kuwapitikitsa m’dziko lino. Ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”+
7 Chotero, akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga malipiro okamulipira kuti awawombezere maula,+ komanso anamuuza zimene Balaki ananena. 8 Balamu atamva mawuwo anawawuza kuti: “Gonani konkuno lero. Ndikuyankhani malinga n’zimene Yehova ati andiuze.”+ Akalonga a ku Mowabuwo anagonadi kwa Balamu.
9 Kenako Mulungu anafika kwa Balamu n’kumufunsa kuti:+ “Kodi anthu uli nawowa ndani?” 10 Balamu anayankha Mulungu woonayo kuti: “Balaki+ mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ndi amene watumiza anthuwa kuti adzandiitane kuti, 11 ‘Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo adzaza dziko lino kulikonse kumene munthu angayang’ane.+ Tsopano bwerani, mudzanditembererere anthuwa,+ kuti mwina ndingathe kumenyana nawo n’kuwathamangitsa.’” 12 Koma Mulungu anauza Balamu kuti: “Usapite nawo, ndipo anthuwo usakawatemberere,+ pakuti iwo ndi odalitsidwa.”+
13 M’mawa mwake Balamu atadzuka, anauza akalonga a Balakiwo kuti: “Pitani kudziko lakwanu, chifukwa Yehova wakana zoti ndipite nanu.” 14 Pamenepo akalonga a ku Mowabu aja ananyamuka n’kubwerera kwa Balaki, ndipo anakamuuza kuti: “Balamu wakana kubwera nafe.”+
15 Koma Balaki anatumizanso akalonga ena, ochulukirapo komanso olemekezeka kuposa oyamba aja. 16 Awanso anapita kwa Balamu n’kumuuza kuti: “Balaki mwana wa Zipori akuti: ‘Chonde, pasakhale chokuletsani kubwera kwa ine. 17 Ndithu ndidzakupatsani ulemerero waukulu,+ ndipo chilichonse chimene mungandiuze ndidzachita.+ Chonde tabwerani mudzanditembererere anthuwa.’” 18 Koma Balamu anayankha atumiki a Balaki aja kuti: “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse mosemphana ndi zimene Yehova Mulungu wanga angandilamule, kaya kuchotsera kapena kuwonjezerapo.+ 19 Bwanji inunso mugone konkuno usiku wa lero, kuti ndimve zimene Yehova andiuze ulendo uno.”+
20 Usikuwo Mulungu anafika kwa Balamu, n’kumuuza kuti: “Ngati anthuwa abwera kudzakuitana, nyamuka, pita nawo limodzi. Koma ukalankhule mawu okhawo amene ndikakuuze.”+ 21 M’mawa kutacha, Balamu anadzuka n’kumanga chishalo pabulu* wake, ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+
22 Tsopano Mulungu anapsa mtima poona kuti Balamu akupita, moti mngelo wa Yehova anaima pamsewu kuti amutchingire njira.+ Balamuyo anali pabulu wake, ndipo anali ndi anyamata ake awiri. 23 Ndiyeno buluyo anaona mngelo wa Yehova ali chilili pamsewu lupanga lake lili m’manja.+ Pamenepo buluyo anayesetsa kupatukira kumbali kwa msewu kuti adutse kutchire, koma Balamu anayamba kum’kwapula kuti am’bwezere mumsewu. 24 Mngelo wa Yehovayo anakaimanso panjira yopanikiza yodutsa pakati pa minda ya mpesa. Njirayo inali ndi khoma la miyala uku ndi uku. 25 Buluyo anaonanso mngelo wa Yehova uja. Ndipo anayamba kudzikanikizira kukhoma, moti anakanikiziranso phazi la Balamu kukhomako. Pamenepo, Balamu anayamba kum’kwapulanso kwambiri bulu uja.
26 Tsopano mngelo wa Yehova anasunthiranso patsogolo. Anakaima pamalo ena opanikiza, pomwe panalibiretu mpata woti n’kudutsira kudzanja lamanja kapena lamanzere. 27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova, tsopano anangokhala pansi, Balamu ali pamsana pake. Pamenepo Balamu anapsa mtima koopsa,+ ndipo anayamba kum’kwapulanso ndi ndodo yake. 28 Potsirizira pake, Yehova anatsegula pakamwa pa buluyo,+ ndipo buluyo anafunsa Balamu kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani kuti mundikwapule katatu konseka?”+ 29 Balamu anayankha buluyo kuti: “Chifukwa wandichita nkhanza kwambiri. Moti ndikanakhala ndi lupanga m’dzanja langa, bwenzi pano n’takupha!”+ 30 Buluyo anafunsanso Balamu kuti: “Kodi si ine bulu wanu amene mwakhala mukukwera moyo wanu wonse mpaka lero? Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi kwa inu?”+ Iye anayankha kuti: “Iyayi!” 31 Tsopano Yehova anatsegula maso a Balamu,+ ndipo iye anaona mngelo wa Yehova ali chilili panjirapo, lupanga lili m’manja. Nthawi yomweyo, Balamu anagwada pansi n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.
32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa uli pa ulendo wothamangira kukachita zotsutsana ndi chifuniro changa.+ 33 Koma buluyu wandiona, ndipo wayesa kundipewa maulendo atatu onsewa.+ Akanapanda kundipewa, ndithu, bwenzi pano n’takupha.+ Koma buluyu n’kanamusiya kuti akhale ndi moyo.” 34 Balamu atamva zimenezi anauza mngelo wa Yehovayo kuti: “Ndachimwa,+ sindinadziwe kuti inuyo munaima pamsewu kudzakumana nane. Bwanji ndibwerere ngati sizinakusangalatseni?” 35 Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa,+ koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.”+ Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo.
36 Balaki atamva kuti Balamu wafika, nthawi yomweyo ananyamuka kukamulandira kumzinda wa Mowabu. Mzindawu unali pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene unali kumalire a dzikolo.+ 37 Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi sindinatumize amithenga kuti adzakuitaneni? Nanga n’chifukwa chiyani simunabwere? Kodi mukuganiza kuti ineyo sindingathe kukupatsani ulemerero wochuluka?”+ 38 Balamu anayankha Balaki kuti: “Si ine ndabwerane! Inetu sindingathe kunena kalikonse.+ Mawu amene Yehova ati aike m’kamwa mwangamu ndi amene ndilankhule.”+
39 Chotero Balamu anatengana ndi Balaki, n’kupita ku Kiriyati-huzoti. 40 Kumeneko Balaki anapereka nsembe za nyama ya ng’ombe ndi nkhosa,+ n’kutumiza ina kwa Balamu ndi akalonga amene anali nawo limodzi. 41 M’mawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu n’kupita naye ku Bamoti-baala.+ Anam’tengera kumeneko kuti akathe kuliona bwino khamu lonse la Aisiraeli.+
23 Tsopano Balamu anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe+ okwanira 7. Mukatero mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.” 2 Nthawi yomweyo Balaki anachita monga momwe anamuuzira Balamu. Kenako, Balaki ndi Balamu anapereka nsembe. Anapereka ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 3 Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Muime pafupi ndi nsembe yanu yopsereza.+ Mundilole ine ndichoke, kuti mwina Yehova akumana nane n’kundilankhula.+ Akatero, zimene andiuzezo n’zimenenso ndinene kwa inu.” Chotero Balamu anapita pamwamba pa phiri.
4 Mulungu atam’peza Balamu,+ iye anamuuza Mulunguyo kuti: “Ndamanga maguwa ansembe 7 m’mizere, ndipo ndapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.”+ 5 Pamenepo Yehova anamuika Balamu+ mawu m’kamwa, n’kumuuza kuti: “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze mawu amenewa.”+ 6 Iye atabwerera kwa Balaki, anapeza Balakiyo limodzi ndi akalonga onse a ku Mowabu ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza. 7 Pamenepo Balamu anayamba kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:
“Balaki mfumu ya Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu,+
Kuchokera kumapiri a kum’mawa, kuti:
‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.
Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+
8 Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?+
Anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka, ndingathe bwanji kuwaitanira tsoka?+
9 Pakuti pomwe ndili pano ndikutha kuwaona, pamwamba pa matanthwe pano,
Ndikuwaona ndithu, pano pamwamba pa mapiri.
Akukhala paokhaokha m’mahema awo,+
Iwo akudziona kuti ndi osiyana ndi mitundu ina.+
10 Ndani watha kuwerenga mtundu wa Yakobo,+ wochuluka ngati fumbi,
Ndipo ndani watha kuwerenga gawo limodzi mwa magawo anayi a Isiraeli?
Moyo wanga ufe imfa ya olungama,+
Ndipo mathero anga akhale ngati awo.”+
11 Balaki atamva zimenezi anafunsa Balamu kuti: “N’chiyani mwandichitachi? Ndinakutengani kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa kwambiri.”+ 12 Koma iye anamuyankha kuti: “Kodi chilichonse chimene Yehova wandiika m’kamwa, si chimene ndinayenera kunena?”+
13 Ndiyeno Balaki anauza Balamu kuti: “Tabwerani chonde, tiyeni tipite kumalo ena kumene mungathe kuwaona anthuwo. Simukaona onse, koma mukangoona okhawo amene ali chakufupi.+ Mukanditembererere amenewo.”+ 14 Chotero anamutengera ku Zofimu, pamwamba pa phiri la Pisiga.+ Kumeneko anamanga maguwa ansembe 7, n’kupereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 15 Pambuyo pake, Balamu anauza Balaki kuti: “Muime pano, pafupi ndi nsembe yanu yopserezayi koma ine mundilole ndichoke ndikalankhule ndi Mulungu uko.” 16 Kumeneko Yehova analankhuladi ndi Balamu, n’kumuika mawu m’kamwa, ndipo anamuuza kuti:+ “Bwerera kwa Balaki+ ukamuuze zimenezi.” 17 Balamu atabwerera kwa Balaki, anam’peza ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza, akalonga a ku Mowabu ali naye limodzi pamenepo. Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi Yehova wati chiyani?” 18 Pamenepo Balamu anayambanso kulankhula mwa ndakatulo, kuti:+
“Nyamuka, Balaki iwe, tamvera.
Tchera khutu kwa ine, iwe mwana wa Zipori.+
19 Mulungu si munthu, woti anganene mabodza,+
Si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu.+
Kodi ananenapo kanthu koma osachita,
Analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?+
21 Iye sanaone mphamvu yamatsenga+ iliyonse ikuchita kanthu pa Yakobo,
Ndipo sanaone Isiraeli akuponyeredwa vuto.
Mulungu wake Yehova ali naye,+
Ndipo mfuu yotamanda mfumu ikumveka pakati pake.
23 Palibe amene walodza Yakobo,+
Ngakhale kuchesa Isiraeli.+
Za Yakobo ndi Isiraeli, adzati,
‘Mwaonatu zimene Mulungu wachita!’+
24 Taonani, mtundu udzadzuka ngati mkango,
Udzanyamuka monga mkango.+
Sugona pansi mpaka ugwire nyama,
Ndipo udzamwa magazi a ophedwawo.”+
25 Tsopano Balaki anauza Balamu kuti: “Ngati mwalephera kuwatemberera ngakhale pang’ono pokha, ndiye musawadalitsenso m’pang’ono pomwe.” 26 Pamenepo Balamu anafunsa Balaki kuti: “Kodi sindinanene kwa inu kuti, ‘Ndichita zokhazo zimene Yehova andiuze’?”+
27 Koma Balaki anauza Balamu kuti: “Chonde tabwerani. Tiyeni tipite kumalo enanso. Mwina kumeneko Mulungu woona angalole kuti munditembererere anthuwa.”+ 28 Balaki atatero, anatengera Balamu pamwamba pa phiri la Peori, loyang’ana ku Yesimoni.+ 29 Kumeneko Balamu+ anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe 7, ndipo mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.”+ 30 Chotero Balaki anachita monga momwe Balamu ananenera. Anapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+
24 Balamu ataona kuti Yehova akungowadalitsa Aisiraeli, sanapitenso kukawafunira tsoka lina lililonse+ mmene anachitira nthawi zina zija.+ M’malomwake, anatembenuka n’kuyang’ana kuchipululu. 2 Pamene Balamu anakweza maso ake n’kuona Aisiraeli ali m’misasa mwa mafuko awo,+ mzimu wa Mulungu unafika pa iye.+ 3 Pamenepo anayamba kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,
Mawu a mwamuna wamphamvu, maso ake ali chitsegukire,+
4 Mawu a iye wakumva zonena za Mulungu,+
Iye amene waona masomphenya a Wamphamvuyonse,+
Pamene anali kugwa pansi, maso ake ali chipenyere.+ Mawu ake akuti:
5 Akongolerenji malo ako okhala Yakobo! Mahema ako n’ngokongola ndithu Isiraeli!+
6 Andanda kukafika kutali ngati zigwa,*+
Ngati minda m’mphepete mwa mtsinje.+
Ngati mitengo ya aloye imene Yehova anabzala,
Ngati mikungudza m’mbali mwa madzi.+
7 Madzi odzaza mitsuko yake iwiri akutayikirabe pansi,
Ndipo mbewu yake ili m’mbali mwa madzi ambiri.+
Mfumu yakenso+ idzakwezeka kuposa Agagi,+
Ndi ufumu wake udzakwezedwa.+
8 Mulungu akum’tulutsa mu Iguputo.
Amathamanga mwaliwiro ngati ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+
Adzameza anthu a mitundu ina, om’pondereza iye,+
9 Iye anagwada pansi. Anagona pansi ngati mkango.
Ngati mkango, ndani angayese kum’dzutsa?+
Odalitsa iwe n’ngodalitsika,+
Ndipo otemberera iwe n’ngotembereredwa.”+
10 Pamenepo Balaki anapsera mtima Balamu n’kuwomba m’manja.+ Kenako anauza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere+ adani anga, koma iwe wawadalitsa kwambiri katatu konseka! 11 Choka! Nyamuka uzipita. Ine ndimati ndikupatse ulemerero,+ koma taona! Yehova wakumanitsa ulemererowo.”
12 Balamu poyankha anafunsa Balaki kuti: “Kodi sindinanene kwa amithenga anu amene munawatuma kwa ine, kuti, 13 ‘Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chochokera mumtima mwanga, kaya chabwino kapena choipa, chosemphana ndi zimene Yehova walamula? Sindinanene kodi, kuti chilichonse chimene Yehova ati alankhule, ndilankhula chomwecho’?+ 14 Chabwino, ndikupita kwa anthu a mtundu wanga. Koma tamverani, ndikuuzeni+ zimene anthuwa adzachite kwa anthu anu kumapeto kwa masiku otsiriza.”+ 15 Kenako anayambanso kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,
Mawu a mwamuna wamphamvu, maso ake ali chitsegukire,+
16 Mawu a munthu womva zonena za Mulungu,+
Iye wozindikira nzeru za Wam’mwambamwamba . . .
Iye anaona masomphenya a Wamphamvuyonse+
Pamene anali kugwa pansi, maso ake ali chipenyere.+ Mawu ake ndi akuti:
17 Ndidzamuona,+ koma si nthawi ino;
Ndidzam’penya, koma si panopo.
Ndithu nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,
Ndodo yachifumu idzatulukadi mu Isiraeli.+
Ndipo iye adzaphwanya chipumi cha Mowabu+
Ndi chigaza cha ana onse ankhondo.
20 Tsopano Balamu ataona Amaleki, anapitiriza mawu ake a ndakatulo, kuti:+
“Amaleki anali woyamba wa anthu a mitundu ina,+
Koma chiwonongeko chake chidzakhaladi mapeto ake.”+
21 Iye ataona Akeni,+ anapitirizanso mawu ake a ndakatulo, kuti:
“Mokhala mwanu ndi mokhazikika, malo okhala inu ali pathanthwe.
22 Koma adzafika wodzanyeketsa Kayini*+ ndi moto.
Kodi udzakhalabe mpaka liti Asuri asanakugwire n’kupita nawe kudziko lina?”+
23 Iye anapitiriza kulankhula mawu ake a ndakatulo, kuti:
“Kalanga ine! Adzapulumuke tsokalo ndani, Mulungu akadzaliponya?+
24 Padzafika zombo zochokera kugombe la Kitimu,+
Ndipo iwo adzasautsa Asuri+ ndithu,
Adzasautsadi Ebere.
Koma iyenso adzawonongeka pamapeto pake.”
25 Tsopano Balamu ananyamuka kumabwerera kwawo.+ Nayenso Balaki ananyamuka kulowera njira yake.
25 Tsopano Aisiraeli anali kukhala ku Sitimu.+ Ali kumeneko, iwo anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2 Akaziwo ankabwera kudzaitana Aisiraeliwo kuti azipita nawo limodzi kokapereka nsembe kwa milungu yawo.+ Kumeneko, Aisiraeliwo ankadya ndi kugwadira milungu ya Amowabuwo.+ 3 Chotero Aisiraeli anayamba kupembedza nawo Baala wa ku Peori.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unawayakira.+ 4 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Gwira onse amene akutsogolera anthuwo, uwaphe ndipo mitembo yawo uindandalike padzuwa pamaso pa Yehova.+ Uchite zimenezo kuti mkwiyo wa Yehova umene wayakira Aisiraeli uchoke.” 5 Chotero Mose anauza oweruza a mu Isiraeli+ kuti: “Aliyense wa inu aphe+ anthu ake amene akukapembedza nawo Baala wa ku Peori.”
6 Kenako anthuwo anangoona mwamuna wina wachiisiraeli+ akubwera ndi mkazi wachimidiyani.+ Anali kubwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Isiraeli. Pa nthawiyi n’kuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako. 7 Koma Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, ataona zimenezi nthawi yomweyo ananyamuka pakati pa khamulo n’kutenga mkondo waung’ono m’dzanja lake. 8 Iye anathamangira mwamuna wachiisiraeli uja mpaka kukalowa m’hema wake n’kubaya* awiriwo ndi mkondowo. Anabaya mwamuna wachiisiraeli limodzi ndi mkaziyo, mpaka mkondowo unakadutsa kumaliseche kwa mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa ana a Isiraeli.+ 9 Amene anaphedwa ndi mliriwo analipo 24,000.+
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11 “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga+ pa ana a Isiraeli, chifukwa sanalekerere konse zoti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Inetu ndikanawafafanizadi ana a Isiraeliwa, chifukwa ndimafuna kuti azikhala odzipereka kwa ine ndekha basi.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, umuuze Pinihasi kuti, ‘Tsopano ndikupangana naye pangano la mtendere. 13 Likhale pangano la unsembe kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale,+ chifukwa sanalekerere zoti anthu azipikisana ndi Mulungu wake,+ ndiponso waphimba machimo a ana a Isiraeli.’”+
14 Dzina la mwamuna wachiisiraeli, amene anaphedwa limodzi ndi mkazi wachimidiyani uja, linali Zimiri mwana wa Salu. Saluyo anali mtsogoleri+ wa nyumba ya makolo a Asimiyoni. 15 Dzina la mkazi wachimidiyani amene anaphedwayo linali Kozibi, mwana wa Zuri.+ Zuri anali mtsogoleri wa fuko la nyumba ina ya makolo ku Midiyani.+
16 Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 17 “Amuna inu, athireni nkhondo Amidiyani, ndipo muwakanthe,+ 18 chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera,+ pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwakanthe ndithu, chifukwanso cha zochita za mlongo wawo Kozibi,+ mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+
26 Mliri+ uja utatha, Yehova analankhula ndi Mose ndi Eleazara mwana wa wansembe Aroni, kuti: 2 “Werengani amuna onse oyenera kupita kunkhondo pakati pa khamu lonse la ana a Isiraeli. Muwerenge kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, potsata nyumba za makolo awo.”+ 3 Chotero Mose ndi wansembe Eleazara+ analankhula ndi Aisiraeliwo m’chipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko,+ kuti: 4 “Werengani ana onse a Isiraeli kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, monga Yehova analamulira Mose.”+
Tsopano ana onse a Isiraeli amene anatuluka m’dziko la Iguputo ndi awa: 5 Rubeni anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli.+ Ana aamuna a Rubeni anali: Hanoki+ amene anali kholo la banja la Ahanoki, Palu+ amene anali kholo la banja la Apalu, 6 Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi, ndi Karami+ amene anali kholo la banja la Akarami. 7 Amenewa anali mabanja a Arubeni. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 43,730.+
8 Mwana wamwamuna wa Palu anali Eliyabu. 9 Ana aamuna a Eliyabu anali Nemueli, Datani+ ndi Abiramu.+ Awiriwa, Datani ndi Abiramu, anali osankhidwa a khamulo. Iwowa ndi amene anagwirizana ndi gulu la Kora+ pokangana ndi Mose ndi Aroni, pamene anali kutsutsana ndi Yehova.
10 Zitatero, nthaka inayasama n’kuwameza.+ Koma Kora anafa pamene moto unanyeketsa gulu la amuna 250.+ Choncho iwowa anakhala chitsanzo chopereka chenjezo.+ 11 Koma ana a Kora sanafe.+
12 Ana aamuna a Simiyoni+ mwa mabanja awo anali awa: Nemueli+ amene anali kholo la banja la Anemueli, Yamini+ amene anali kholo la banja la Ayamini, Yakini+ amene anali kholo la banja la Ayakini, 13 Zera amene anali kholo la banja la Azera, ndi Shauli+ amene anali kholo la banja la Ashauli. 14 Amenewa ndiwo anali mabanja a Asimiyoni. Amuna onse pamodzi analipo 22,200.+
15 Ana aamuna a Gadi+ ndi mabanja awo anali awa: Zefoni amene anali kholo la banja la Azefoni, Hagi amene anali kholo la banja la Ahagi, Suni amene anali kholo la banja la Asuni, 16 Ozini amene anali kholo la banja la Aozini, Eri amene anali kholo la banja la Aeri, 17 Arodi amene anali kholo la banja la Aarodi, ndi Areli+ amene anali kholo la banja la Aareli. 18 Amenewa ndiwo anali mabanja a ana a Gadi. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 40,500.+
19 Ana a Yuda+ anali Ere+ ndi Onani.+ Koma awiriwa anafera m’dziko la Kanani.+ 20 Choncho ana aamuna a Yuda mwa mabanja awo anali awa: Shela+ amene anali kholo la banja la Ashela, Perezi+ amene anali kholo la banja la Aperezi, ndi Zera+ amene anali kholo la banja la Azera. 21 Ana aamuna a Perezi anali Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi, ndi Hamuli+ amene anali kholo la banja la Ahamuli. 22 Amenewa ndiwo anali mabanja a Yuda.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 76,500.+
23 Ana aamuna a Isakara+ ndi mabanja awo anali awa: Tola+ amene anali kholo la banja la Atola, Puva amene anali kholo la banja la Apuna, 24 Yasubi amene anali kholo la banja la Ayasubi, ndi Simironi+ amene anali kholo la banja la Asimironi. 25 Amenewa ndiwo anali mabanja a Isakara. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 64,300.+
26 Ana aamuna a Zebuloni+ anali awa: Seredi amene anali kholo la banja la Aseredi, Eloni amene anali kholo la banja la Aeloni, ndi Yahaleeli+ amene anali kholo la banja la Ayahaleeli. 27 Amenewa ndiwo anali mabanja a Azebuloni. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 60,500.+
28 Ana aamuna a Yosefe+ ndi mabanja awo anali Manase ndi Efuraimu.+ 29 Ana aamuna a Manase+ anali Makiri+ amene anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anabereka Giliyadi.+ Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi. 30 Ana aamuna a Giliyadi anali awa: Yezeri+ amene anali kholo la banja la Ayezeri, Heleki amene anali kholo la banja la Aheleki, 31 Asiriyeli amene anali kholo la banja la Aasiriyeli, Sekemu amene anali kholo la banja la Asekemu, 32 Semida+ amene anali kholo la banja la Asemida, ndi Heferi+ amene anali kholo la banja la Aheferi. 33 Koma Tselofekadi, mwana wamwamuna wa Heferi, analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha.+ Mayina a ana aakazi a Tselofekadi anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.+ 34 Amenewa ndiwo anali mabanja a Manase. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 52,700.+
35 Ana aamuna a Efuraimu+ ndi mabanja awo anali awa: Sutela+ amene anali kholo la banja la Asutela, Bekeri amene anali kholo la banja la Abekeri, ndi Tahani+ amene anali kholo la banja la Atahani. 36 Ana aamuna a Sutela anali Erani amene anali kholo la banja la Aerani. 37 Amenewa ndiwo anali mabanja a ana a Efuraimu.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 32,500. Awa anali ana aamuna a Yosefe ndi mabanja awo.+
38 Ana aamuna a Benjamini+ ndi mabanja awo anali awa: Bela+ amene anali kholo la banja la Abela, Asibeli+ amene anali kholo la banja la Aasibeli, Ahiramu amene anali kholo la banja la Aahiramu, 39 Sefufamu amene anali kholo la banja la Asefufamu, ndi Hufamu+ amene anali kholo la banja la Ahufamu. 40 Ana aamuna a Bela anali Aridi ndi Namani.+ Aridi anali kholo la banja la Aaridi. Namani anali kholo la banja la Anamani. 41 Amenewa ndiwo anali ana aamuna a Benjamini+ ndi mabanja awo. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 45,600.+
42 Ana aamuna a Dani+ mwa mabanja awo anali ochokera kwa Suhamu amene anali kholo la banja la Asuhamu. Awa anali mabanja a Dani+ potsata fuko lawo. 43 Amuna onse owerengedwa m’mabanja onse a Asuhamu analipo 64,400.+
44 Ana aamuna a Aseri+ ndi mabanja awo anali awa: Imuna+ amene anali kholo la banja la Aimuna, Isivi+ amene anali kholo la banja la Aisivi ndi Beriya amene anali kholo la banja la Aberiya. 45 Ana aamuna a Beriya anali Hiberi amene anali kholo la banja la Ahiberi, ndi Malikieli+ amene anali kholo la banja la Amalikieli. 46 Mwana wamkazi wa Aseri anali Sera.+ 47 Amenewa ndiwo anali mabanja a ana aamuna a Aseri.+ Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 53,400.+
48 Ana aamuna a Nafitali+ ndi mabanja awo anali awa: Yahazeeli+ amene anali kholo la banja la Ayahazeeli, Guni+ amene anali kholo la banja la Aguni, 49 Yezera+ amene anali kholo la banja la Ayezera, ndi Silemu+ amene anali kholo la banja la Asilemu. 50 Amenewa ndiwo anali mabanja a Nafitali+ potsata fuko lawo. Amuna onse owerengedwa m’mabanja awo analipo 45,400.+
51 Amenewa ndiwo amuna onse amene anawerengedwa pakati pa ana a Isiraeli. Onse pamodzi analipo 601,730.+
52 Pambuyo pake, Yehova analankhula ndi Mose kuti: 53 “Anthu amenewa uwagawire dzikoli malinga ndi chiwerengero cha mayinawo, kuti likhale cholowa chawo.+ 54 Amene ali ndi anthu ambiri apatsidwe dziko lalikulu monga cholowa chake, ndipo amene ali ndi anthu ochepa apatsidwe dziko laling’ono monga cholowa chake.+ Aliyense apatsidwe cholowacho malinga ndi chiwerengero cha anthu ake. 55 Njira yokha imene ugawire dzikolo ndiyo mwa kuchita maere basi.+ Onse alandire cholowacho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56 Mtsogoleri wa fuko aliyense um’gawire cholowa chake mwa kuchita maere, amene ali ndi anthu ochuluka kapena anthu ochepa.”
57 Tsopano awa ndi mayina a amuna owerengedwa mwa Alevi+ malinga ndi mabanja awo: Agerisoni, a banja la Gerisoni,+ Akohati, a banja la Kohati,+ ndi Amerari, a banja la Merari.+ 58 Nawa mabanja a Alevi: banja la Alibini,+ banja la Aheburoni,+ banja la Amali,+ banja la Amusi,+ ndi banja la Akora.+
Kohati+ anabereka Amuramu.+ 59 Mkazi wa Amuramu anali Yokebedi,+ mwana wa Levi, amene mkazi wake anam’berekera ku Iguputo. Yokebedi anaberekera Amuramu ana awa: Aroni, Mose ndi mlongo wawo Miriamu.+ 60 Ndiyeno Aroni anabereka Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+ 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa chifukwa chofukiza moto wosaloleka pamaso pa Yehova.+
62 Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo.+ Iwowa sanawerengedwe limodzi ndi ana a Isiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa ana a Isiraeli.+
63 Awa ndiwo anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa ana a Isiraeli. Anawawerengera m’chipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko.+ 64 Koma pakati pa amenewa, panalibe aliyense wa amene anawerengedwa m’chipululu cha Sinai aja, pamene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga ana a Isiraeli.+ 65 Zinakhala choncho chifukwa ponena za iwo, Yehova anati: “Mulimonsemo adzafera m’chipululu basi.”+ Choncho, sipanatsale ndi mmodzi yemwe kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
27 Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri, ndipo Makiri anali mwana wa Manase.+ Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewo mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.+ 2 Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, pamaso pa wansembe Eleazara,+ pamaso pa atsogoleri ndi khamu lonse, pakhomo la chihema chokumanako, n’kunena kuti: 3 “Bambo athu anafera m’chipululu.+ Koma iwo sanali nawo m’gulu la Kora+ limene linasonkhana kuti litsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo,+ ndipo pa nthawiyo analibe mwana aliyense wamwamuna. 4 Kodi dzina la bambo athu lichotsedwe ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna?+ Chonde, tipatseni cholowa pakati pa abale awo a bambo athu.”+ 5 Pamenepo, Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+
6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 7 “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo monga cholowa chawo, pakati pa abale a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.+ 8 Ndipo ulankhule kwa ana a Isiraeli kuti: ‘Mwamuna akamwalira wopanda mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. 9 Ngati iye analibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene* ake. 10 Ngati analibe azichimwene, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene a bambo ake. 11 Ngati bambo ake analibe azichimwene awo, muzipereka cholowa chake kwa wachibale wake wapafupi wa ku banja lawo,+ ndipo azitenga cholowacho kukhala chake. Ili likhale lamulo kwa ana a Isiraeli mwa chigamulo changa, monga Yehova walamulira Mose.’”
12 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Kwera phiri ili la Abarimu,+ ukaone dziko limene ndidzalipereke kwa ana a Isiraeli.+ 13 Pambuyo poliona dzikolo, udzaikidwa m’manda kuti ukagone ndi makolo ako.+ Ndithudi, iweyo udzaikidwa m’manda mofanana ndi Aroni m’bale wako,+ 14 chifukwa amuna inu munapandukira mawu anga m’chipululu cha Zini, pa nthawi imene khamu lija linakangana nanu.+ Munalephera kundilemekeza+ pa madzi amene anatuluka patsogolo pa khamulo, madzi a Meriba+ ku Kadesi,+ m’chipululu cha Zini.”+
15 Tsopano Mose anauza Yehova kuti: 16 “Inu Yehova, Mulungu wa miyoyo ya zamoyo+ zamitundu yonse,+ sankhani munthu woti aziyang’anira khamuli.+ 17 Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse,+ kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda m’busa.”+ 18 Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,*+ ndipo uike manja ako pa iye.+ 19 Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara, ndi pamaso pa khamu lonse, ndipo umuike kukhala mtsogoleri pamaso pawo.+ 20 Um’patseko ulemerero wako,+ kuti khamu lonse la ana a Isiraeli lizimumvera.+ 21 Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira+ chigamulo cha Yehova m’malo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Yoswa akalamula, ana onse a Isiraeli ndi khamu lonse azituluka naye, ndipo akalamulanso, onsewo azibwerako limodzi naye.”
22 Mose anachitadi monga mmene Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa n’kumuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara,+ ndi pamaso pa khamu lonselo. 23 Kenako anaika manja ake pa iye n’kumuika kukhala mtsogoleri+ monga Yehova ananenera kudzera kwa Moseyo.+
28 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 2 “Lamula ana a Isiraeli kuti, ‘Muzionetsetsa kuti pa nthawi yake yoikidwiratu+ mukupereka kwa ine nsembe yanga, yomwe ndi chakudya changa+ chotentha ndi moto, chotulutsa fungo londikhazika mtima pansi.’+
3 “Uwauze kuti, ‘Muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha ndi moto motere: Tsiku lililonse muzipereka nsembe yopsereza ya ana a nkhosa awiri amphongo, achaka chimodzi ndi opanda chilema.+ 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzim’pereka nsembe m’mawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzim’pereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,+ monga nsembe yambewu.+ Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.+ 6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova monga nsembe yafungo lokhazika mtima pansi, yotentha ndi moto.+ 7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa+ chokwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo+ aliyense muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsayo+ m’malo oyera. 8 Mwana wa nkhosa wamphongo winayo muzim’pereka nsembe madzulo kuli kachisisira. Muzim’pereka limodzi ndi nsembe yambewu ndiponso yachakumwa, mofanana ndi nsembe ya m’mawa ija. Izikhala nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
9 “‘Koma pa tsiku la sabata,+ muzipereka nsembe ana a nkhosa awiri amphongo opanda chilema. Muziwapereka pamodzi ndi ufa wosalala monga nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta, ndipo uzikhala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Muziperekanso nsembe yake yachakumwa. 10 Imeneyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku lasabata, yoperekedwa pa tsiku la sabata lililonse. Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, pamodzi ndi nsembe yake yachakumwa.+
11 “‘Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ 12 Pang’ombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu.+ Ufawo uzikhala wothira mafuta. Nkhosa yamphongo imodziyo+ muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Ufawo uzikhala wothira mafuta. 13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yomwe ndi nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi,+ nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 14 Panyama iliyonse yoperekedwa nsembe muziperekanso nsembe yachakumwa. Ng’ombe yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana hafu+ ya muyezo wa hini. Nkhosa yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu+ a muyezo wa hini. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo muzim’pereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo anayi+ a muyezo wa hini. Zinthu zimenezi muzizipereka monga nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, yoperekedwa mwezi uliwonse pa miyezi yonse ya pa chaka.+ 15 Muziperekanso mwana wa mbuzi+ monga nsembe yamachimo kwa Yehova, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.+
16 “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14, pazikhala pasika wa Yehova.+ 17 Ndiyeno pa tsiku la 15 la mwezi umenewu pazikhala chikondwerero. Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda chofufumitsa.+ 18 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+ 19 Muzipereka nsembe yotentha ndi moto, yomwe ndi nsembe yopsereza+ kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+ 20 Nsembe zake zambewu+ muzizipereka motere: Ng’ombe yamphongo iliyonse muziipereka limodzi ndi ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Nkhosa yamphongoyo muziipereka limodzi ndi ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ Ufawo uzikhala wothira mafuta. 21 Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense pa ana a nkhosa 7 amenewo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo+ wa efa. 22 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuti ikhale yophimbira machimo anu.+ 23 Muzipereka nsembe zimenezi, kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya m’mawa ya tsiku ndi tsiku.+ 24 Mofanana ndi zimenezi, muziperekanso nsembe yotentha ndi moto tsiku lililonse kwa masiku 7, monga chakudya+ cha Yehova, monganso nsembe yafungo lokhazika mtima pansi kwa iye.+ Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, ndi nsembe yake yachakumwa. 25 Pa tsiku la 7 muzikhala ndi msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+
26 “‘Ndipo pa tsiku la zipatso zoyambirira,+ pamene muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova, paphwando lanu la masabata,+ muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse pa tsikuli.+ 27 Muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe ziwiri zazing’ono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, achaka chimodzi.+ 28 Muziperekanso nsembe yake yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ng’ombe yamphongo iliyonse. Pankhosa yamphongo imodziyo, muzipereka ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10+ a muyezo wa efa. 29 Pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo, muzipereka ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10+ a muyezo wa efa. 30 Komanso muzipereka mwana wa mbuzi wophimbira machimo anu.+ 31 Muzipereka zimenezi+ kuwonjezera pa nsembe yanu yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu. Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+ Muziperekanso nsembe yake yachakumwa.+
29 “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Lizikhala tsiku lanu loliza lipenga.+ 2 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 3 Muziperekanso ufa wosalala wothira mafuta monga nsembe zake zambewu. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pang’ombe yamphongoyo, magawo awiri mwa magawo 10 pankhosa yamphongoyo,+ 4 ndi gawo limodzi mwa magawo 10 pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7+ amenewo. 5 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wamphongo, monga nsembe yamachimo yophimbira machimo anu.+ 6 Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo malinga ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zotentha ndi moto zopereka fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
7 “‘Pa tsiku la 10 la mwezi wa 7 umenewu, muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzidzisautsa.*+ Musamagwire ntchito yamtundu uliwonse.+ 8 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+ 9 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Popereka ng’ombe yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongoyo+ muziperekanso ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 10 Popereka aliyense wa ana a nkhosa 7 amphongowo,+ muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 11 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yamachimo pa tsiku lophimba machimo, ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe zake zambewu ndiponso zachakumwa.+
12 “‘Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7,+ muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Muzichita chikondwerero kwa Yehova masiku 7.+ 13 Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembe imeneyo izikhala ya ng’ombe 13 zazing’ono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazi n’zopanda chilema.+ 14 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Iliyonse ya ng’ombe 13 zamphongozo muziiperekera ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Iliyonse ya nkhosa zamphongo ziwirizo muziiperekera ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 15 Aliyense wa ana a nkhosa 14 amphongowo, muzim’perekera ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 16 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
17 “‘Pa tsiku lachiwiri, muzipereka ng’ombe 12 zazing’ono zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 18 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 19 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu, limodzi ndi nsembe zake zachakumwa.+
20 “‘Pa tsiku lachitatu, muzipereka ng’ombe 11 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 21 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 22 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.
23 “‘Pa tsiku lachinayi, muzipereka ng’ombe 10 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 24 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 25 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
26 “‘Pa tsiku lachisanu, muzipereka ng’ombe 9 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 27 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 28 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
29 “‘Pa tsiku la 6, muzipereka ng’ombe 8 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 30 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 31 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
32 “‘Pa tsiku la 7, muzipereka ng’ombe 7 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 33 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse la zimenezi.+ 34 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
35 “‘Pa tsiku la 8, muzichita msonkhano wapadera.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ 36 Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 37 Popereka nyama zimenezi, ng’ombe yamphongo, nkhosa yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 38 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
39 “‘Muzipereka zimenezi kwa Yehova pa zikondwerero zanu.+ Muzizipereka kuwonjezera pa zopereka zanu zalonjezo,+ ndi nsembe zanu zaufulu+ zimene mumapereka monga nsembe zanu zopsereza,+ nsembe zanu zambewu,+ nsembe zanu zachakumwa,+ ndi nsembe zanu zachiyanjano.’”+ 40 Pamenepo Mose anauza ana a Isiraeli zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+
30 Ndiyeno Mose analankhula ndi atsogoleri+ a mafuko a ana a Isiraeli, kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula: 2 Munthu akalonjeza+ kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana,+ asalephere kukwaniritsa mawu ake.+ Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.+
3 “Mtsikana amene akanali m’nyumba ya bambo ake akalonjeza zinazake kwa Yehova,+ kapena akachita lonjezo lodzimana, 4 bambo ake n’kumumva ndithu akulonjeza kapena akuchita lonjezo lodzimanalo,+ koma osanenapo kanthu, malonjezo ake onsewo akhale momwemo. Zikatero, lonjezo lake lililonse lodzimana likhale momwemo. 5 Koma ngati bambo ake am’kaniza pa tsiku limene amva malonjezo ake onse, malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, akhale opanda ntchito. Yehova adzam’khululukira chifukwa bambo ake anam’kaniza.+
6 “Koma ngati mkaziyo ali wokwatiwa, ndipo akuchita lonjezo mwa kulumbirira moyo wake,+ kapena kulonjeza ndi pakamwa pake mosaganizira bwino, 7 mwamuna wake n’kumva koma osanena kanthu kwa iye pa tsiku limene wamva mawu a lonjezolo, malonjezo ake a kudzimana amene walumbirira moyo wake akhale momwemo.+ 8 Mwamunayo akam’kaniza pa tsiku limene wamva kulonjezako,+ ndiye kuti wafafaniza lonjezo la mkaziyo, kapena lonjezo lake limene anachita mosaganizira bwino, limene analumbirira moyo wake ndi pakamwa pake. Yehova adzam’khululukira mkaziyo.+
9 “Koma mkazi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akachita lonjezo, lonjezo lililonse limene walumbirira moyo wake likhale momwemo.
10 “Komabe, ngati mkazi walonjeza ali m’nyumba ya mwamuna wake, kapena ngati wachita lonjezo lodzimana+ mwa kulumbirira moyo wake, 11 mwamuna wake n’kumva koma osanenapo kanthu, osam’kaniza, malonjezo ake onse akhale momwemo, ndipo lonjezo lililonse lodzimana limene walumbirira moyo wake likhale momwemo. 12 Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva mawu alionse otuluka pakamwa pa mkaziyo, mawu olonjezerawo kapena malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, malonjezo a mkaziyo akhale opanda ntchito.+ Mwamuna wake wawafafaniza, ndipo Yehova adzam’khululukira mkaziyo.+ 13 Mwamuna wake ali ndi mphamvu zokhazikitsa kapena kufafaniza lonjezo lililonse la mkazi wake, kapenanso lumbiro la mkaziyo lodzimana, losautsa moyo wake.+ 14 Koma ngati mwamunayo sananenepo kanthu kwa mkazi wake, masiku n’kumapita, ndiye kuti mwamunayo wakhazikitsa malonjezo onse a mkaziyo, kapena malonjezo onse odzimana amene mkaziyo walumbirira moyo wake.+ Iye wawakhazikitsa chifukwa sananenepo kanthu kwa mkaziyo pa tsiku limene anamumva akulonjeza. 15 Ndipo ngati mwamunayo afafaniza malonjezowo patapita nthawi pambuyo poti wawamva kale, cholakwa chizikhala pa iyeyo m’malo mwa mkazi wake.+
16 “Awa ndiwo malangizo amene Yehova anapatsa Mose okhudza mwamuna ndi mkazi wake,+ ndiponso bambo ndi mwana wake wachitsikana amene akukhalabe m’nyumba mwake.”+
31 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Uwabwezere+ Amidiyani+ pa zimene anachitira ana a Isiraeli. Pambuyo pake udzaikidwa m’manda kuti ukagone ndi makolo ako.”+
3 Chotero Mose analankhula ndi anthuwo, kuti: “Konzekeretsani amuna pakati panu, apite kunkhondo. Apite kukamenyana ndi Amidiyani, kuti Yehova awalange Amidiyaniwo pobwezera zimene anachita.+ 4 Mutenge amuna 1,000 pa fuko lililonse la mafuko onse a Isiraeli kuti apite kunkhondo.” 5 Choncho amuna 1,000 anatengedwa pa fuko lililonse mwa masauzande+ a Aisiraeliwo. Amuna onse opita kunkhondo anakwana 12,000.+
6 Ndiyeno Mose anatumiza amunawo kunkhondo, amuna 1,000 pa fuko lililonse. Anawatumiza limodzi ndi Pinihasi,+ mwana wa wansembe Eleazara. Pinihasi ananyamula ziwiya zopatulika ndi malipenga+ operekera zizindikiro. 7 Amunawo anakathira nkhondo Amidiyani, monga mmene Yehova analamulira Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense.+ 8 Anaphanso mafumu asanu achimidiyani.+ Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga. 9 Koma akazi achimidiyani ndi ana awo anawagwira ndi kuwatenga kupita nawo kwawo.+ Anafunkhanso ziweto zawo zonse ndi chuma chawo chonse. 10 Mizinda yawo yonse imene anali kukhalamo, ndi misasa yawo yonse ya mipanda anaitentha ndi moto.+ 11 Anatenga zonse zimene anafunkha,+ zomwe zinaphatikizapo anthu ndi ziweto zomwe. 12 Anatengera anthu ogwidwawo limodzi ndi zofunkha zina zonse kwa Mose, wansembe Eleazara, ndi kwa khamu la ana a Isiraeli. Anapita nawo kumsasa wawo ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+
13 Atafika nawo kumeneko, Mose ndi wansembe Eleazara, limodzi ndi atsogoleri onse a anthuwo, anatuluka kukakumana nawo kunja kwa msasa. 14 Koma Mose anakwiya nawo kwambiri atsogoleri a nkhondowo,+ atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100, amene anachokera kunkhondo. 15 Ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi akazi onse mwawasiya amoyo?+ 16 Kodi mwaiwala kuti akaziwa ndi amene anatsatira mawu a Balamu? Si ndiwo kodi amene ananyengerera ana a Isiraeli kuti achimwire Yehova pa zochitika za ku Peori,+ kuti mliri ugwere khamu la anthu a Yehova?+ 17 Tsopano iphani mwana wamwamuna aliyense pakati pa anawa, ndiponso muphe mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna.+ 18 Koma ana aakazi onse aang’ono amene sanagonepo ndi mwamuna musawaphe.+ 19 Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu,+ ndi aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ nonsenu, mudziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo. 20 Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chilichonse chopangidwa ndi ubweya wa mbuzi, ndi chilichonse chopangidwa ndi mtengo.”+
21 Tsopano wansembe Eleazara anauza asilikali amene anapita kunkhondo aja kuti: “Tamverani zimene Yehova analamula Mose, 22 ‘Zinthu zagolide, zasiliva, zamkuwa, zachitsulo, zatini ndi zamtovu, 23 chilichonse chimene sichingapse ndi moto,+ chidutse pamoto kuti chikhale choyera. Muchiyeretsenso ndi madzi.+ Koma chilichonse chimene chingapse ndi moto muchiyeretse ndi madzi.+ 24 Mudzachape zovala zanu pa tsiku la 7 kuti mudzakhale oyera, pambuyo pake mudzalowe mumsasa.’”+
25 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: 26 “Iweyo ndi wansembe Eleazara ndi atsogoleri a khamulo, mutenge zofunkha zonse, zomwe zikuphatikizapo anthu ndi ziweto. 27 Zofunkhazo muzigawe pawiri. Hafu iperekedwe kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, ndipo hafu inayo iperekedwe kwa khamu la anthuwo.+ 28 Monga msonkho+ kwa Yehova, pa gawo loperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ng’ombe, abulu, ndi nkhosa. 29 Zimenezi muzitenge pa hafu imene iwo ati alandire, ndipo muzipereke kwa wansembe Eleazara monga chopereka kwa Yehova.+ 30 Pa hafu imene ana a Isiraeli ati alandire, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu, ng’ombe, abulu, ndi nkhosa, ndi pa ziweto za mtundu uliwonse. Muzipereke kwa Alevi,+ amene amatumikira pachihema cha Yehova chopatulika.”+
31 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara anachita monga Yehova analamulira Mose. 32 Zofunkha zonse zimene analanda amene anapita kunkhondowo zinalipo nkhosa 675,000, 33 ng’ombe 72,000, 34 ndi abulu 61,000. 35 Anthu onse,+ kutanthauza atsikana amene sanagonepo ndi mwamuna,+ analipo 32,000. 36 Pa hafu imene inapatsidwa kwa amuna omwe anapita kunkhondo panali nkhosa 337,500. 37 Pa nkhosa zimenezi, 675 zinali za msonkho+ wa Yehova. 38 Pa hafuyo, ng’ombe zinalipo 36,000. Pa ng’ombe zimenezi, 72 zinali za msonkho wa Yehova. 39 Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anali a msonkho wa Yehova. 40 Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anali a msonkho wa Yehova. 41 Ndiyeno Mose anapereka msonkhowo kwa wansembe Eleazara+ ngati chopereka kwa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.+
42 Pa hafu imene Mose anagawira ana a Isiraeli, pa zofunkha zobwera ndi amuna ochokera kunkhondo, panali izi: 43 Nkhosa 337,500, 44 ng’ombe 36,000, 45 abulu 30,500, 46 ndipo anthu analipo 16,000. 47 Ndiyeno pa hafu yoperekedwa kwa ana a Isiraeliyo, Mose anatengapo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu ndi pa ziweto. Zimenezi anazipereka kwa Alevi+ otumikira pachihema cha Yehova chopatulika,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.
48 Tsopano atsogoleri a masauzande a asilikali+ anafika kwa Mose. Iwowa anali atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100.+ 49 Atafika kwa Mose anati: “Atumiki anufe tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayang’anira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.+ 50 Tsopano lolani kuti aliyense wa ife apereke zimene wabwera nazo monga chopereka kwa Yehova,+ zinthu zagolide, matcheni ovala m’miyendo, zibangili, mphete zachifumu,+ ndolo,* ndi zodzikongoletsera zina za akazi.+ Tipereke zimenezi kwa Yehova kuti ziphimbe machimo athu.”
51 Chotero Mose ndi wansembe Eleazara analandira golideyo kwa iwo,+ kutanthauza zokongoletsera zonse zamtengo wapatali. 52 Golide yense amene anam’pereka kwa Yehova anakwana masekeli 16,750. Uyu ndiye golide amene anaperekedwa ndi atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100. 53 Aliyense wa amuna amene anapita kunkhondowo anabwerako ndi zofunkha zake.+ 54 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira zinthu zagolidezo kwa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100. Ndipo zinthu zagolidezo anakaziika m’chihema chokumanako, kuti zikhale chikumbutso+ kwa ana a Isiraeli pamaso pa Yehova.
32 Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anakhala ndi ziweto zambiri, zankhaninkhani. Iwo anayamba kusirira dziko la Yazeri+ ndi la Giliyadi, ndipo deralo linalidi malo abwino a ziweto. 2 Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo anafika kwa Mose, wansembe Eleazara, ndi atsogoleri a khamulo, n’kuwauza kuti: 3 “Midzi ya Ataroti,+ Diboni,+ Yazeri, Nimira,+ Hesiboni,+ Eleyale,+ Sebamu, Nebo,+ ndi Beoni,+ 4 ndilo dziko limene Yehova anagonjetsera+ khamu la Isiraeli. Dziko limeneli n’labwino kwa ziweto, ndipo atumiki anufe ziweto tili nazo.”+ 5 Anapitiriza kunena kuti: “Ngati mungatikomere mtima atumiki anufe, mutipatse dzikolo ngati cholowa chathu. Tisawoloke nawo Yorodano.”+
6 Koma Mose poyankha, anafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo kuti: “Mukuti abale anu apite kunkhondo inuyo mutsale kuno?+ 7 N’chifukwa chiyani mukufuna kuwatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asawolokere kudziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa? 8 N’zimenenso makolo anu anachita+ ku Kadesi-barinea,+ pamene ndinawatuma kuti akazonde dziko. 9 Iwo atafika kuchigwa* cha Esikolo+ n’kuliona dzikolo, anatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asakalowe m’dziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+ 10 Pa tsiku limenelo Yehova anakwiya koopsa, ndipo analumbira+ kuti, 11 ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ sadzaiona nthaka imene ndinalumbirira Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12 Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaiona nthakayo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’ 13 Yehova anawakwiyira koopsa Aisiraeli ndipo anawachititsa kuzungulira m’chipululu zaka 40,+ mpaka m’badwo wonse wochita zoipa pamaso pa Yehova utatha.+ 14 Inunso mukukhala kam’badwo ka anthu ochita zoipa mofanana ndi makolo anu, kuti muwonjezere mkwiyo woyaka moto wa Yehova+ pa Isiraeli. 15 Mukaleka kumumvera,+ ndithu iye adzachititsanso anthu onsewa kukhalabe m’chipululu muno,+ ndipo mudzawazunzitsa kwambiri.”+
16 Kenako iwo anafikanso kwa iye n’kunena kuti: “Mutilole timange makola amiyala a ziweto zathu kunoko, ndi mizinda ya ana athu aang’ono. 17 Ifeyo tinyamula zida zathu n’kufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo+ ndipo titsogolera ana a Isiraeli kunkhondo mpaka tikawafikitse kumalo awo. Koma ana athu aang’ono tiwasiye m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kuti tiwateteze kwa anthu a dziko lino. 18 Sitidzabwerera kunyumba zathu mpaka aliyense wa ana a Isiraeli atapeza malo ake monga cholowa chake.+ 19 Ife sitidzalandira nawo cholowa tsidya ilo la Yorodano kupita kutsogoloko, chifukwa cholowa chathu chili tsidya lino la Yorodano, kum’mawa kuno.”+
20 Pamenepo Mose anawauza kuti: “Muchitedi zimenezo. Mutenge zida n’kukonzekera kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova.+ 21 Aliyense wokonzekera nkhondo awoloke Yorodano pamaso pa Yehova, kufikira iye atapitikitsa adani ake pamaso pake,+ 22 mpaka dzikolo litagonjetsedwa pamaso pa Yehova.+ Pambuyo pake mudzabwerere.+ Ngati muchitadi zimenezi, mudzakhala opanda mlandu kwa Yehova ndi kwa Isiraeli. Ndipo dzikoli lidzakhaladi lanu, monga cholowa chanu pamaso pa Yehova.+ 23 Koma mukapanda kuchita zimenezo, ndithu mudzachimwira Yehova.+ Ndipo mukatero, dziwani kuti tchimo lanu lidzakutsatani.+ 24 Mizinda ya ana anu aang’ono, ndi makola amiyala a ziweto zanu, mangani. Koma zonse zimene mwalonjeza muchitedi.”+
25 Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anamuyankha Mose kuti: “Atumiki anufe tichita zonse zimene mwalamula mbuyathu.+ 26 Ana athu aang’ono ndi akazi athu atsala kuno m’mizinda ya Giliyadi, limodzi ndi ziweto zathu zonse.+ 27 Koma atumiki anufe tiwoloka, aliyense atakonzekera kukamenya nkhondo+ pamaso pa Yehova, monga mwanenera mbuyathu.”
28 Chotero Mose anapereka lamulo lonena za iwowo kwa wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli. 29 Iye anawauza kuti: “Ana a Gadi ndi ana a Rubeni akawoloka nanu Yorodano, aliyense wokonzekera kukamenya nkhondo+ pamaso pa Yehova, ndipo ngati dzikolo lidzagonjetsedwa pamaso panu, pamenepo mudzawapatse dziko la Giliyadi monga cholowa chawo.+ 30 Koma akapanda kukonzekera nkhondo ndi kuwoloka nanu, basi azikakhala pakati panu m’dziko la Kanani.”+
31 Ana a Gadi ndi ana a Rubeni atamva mawuwo anati: “Tidzachita zimene Yehova walankhula kwa atumiki anufe.+ 32 Tidzawoloka ndi zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova kudziko la Kanani.+ Ndipo tidzalandira cholowa chathu tsidya lino la Yorodano.”+ 33 Pamenepo Mose anagawira malo ana a Gadi+ ndi ana a Rubeni.+ Anagawiranso malo hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawagawira malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, ndi a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana, dera lonse la mizinda ndi midzi yozungulira.
34 Tsopano ana a Gadi anayamba kumanga mizinda ya Diboni,+ Ataroti,+ Aroweli,+ 35 Atiroti-sofani, Yazeri,+ Yogebeha,+ 36 Beti-nimira,+ ndi Beti-harana.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri,+ komanso inali ndi makola a ziweto amiyala.+ 37 Ana a Rubeni anamanga mizinda ya Hesiboni,+ Eleyale,+ Kiriyataimu,+ 38 Nebo,+ Baala-meoni,+ ndi Sibima. Mayina a mizindayi anawasintha, n’kuipatsa mayina ena atsopano.
39 Kenako ana a Makiri+ mwana wa Manase, ananyamuka ulendo wopita kumzinda wa Giliyadi. Analanda mzindawo ndi kupitikitsa Aamori amene anali kukhalamo. 40 Choncho Mose anapereka mzinda wa Giliyadi kwa Makiri mwana wa Manase, ndipo iye anayamba kukhala mmenemo.+ 41 Yairi mwana wa Manase ananyamuka ulendo wokalanda midzi yawo ing’onoing’ono. Midzi imeneyi anaitcha kuti Havoti-yairi.+ 42 Noba nayenso ananyamuka ulendo wokalanda mzinda wa Kenati+ ndi midzi yake yozungulira. Mzindawo anaupatsa dzina lake, loti Noba.
33 Tsopano nawa malo amene ana a Isiraeli anaima pa ulendo wawo, atatuluka mu Iguputo+ m’magulu awo+ motsogoleredwa ndi Mose ndi Aroni.+ 2 Molamulidwa ndi Yehova, Mose anali kulemba malo onyamukira ulendo uliwonse. Maulendowo, kuchokera kumalo ena kukafika kumalo ena, anali awa: + 3 Ananyamuka ku Ramese+ m’mwezi woyamba,+ pa tsiku la 15. Pasika anali atachitika dzulo lake,+ pamene ana a Isiraeli ananyamuka molimba mtima* pamaso pa Aiguputo onse.+ 4 Pa nthawiyi n’kuti Aiguputo ali pa ntchito yoika m’manda ana onse oyamba kubadwa,+ amene Yehova anawapha pakati pawo. Yehovayo anali atapereka ziweruzo pamilungu yawo.+
5 Chotero ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ n’kukamanga msasa ku Sukoti.+ 6 Atanyamuka ku Sukoti anakamanga msasa ku Etamu,+ pafupi ndi chipululu. 7 Atanyamuka ku Etamu anabwerera m’mbuyo kulowera ku Pihahiroti.+ Pihahiroti anali moyang’anana ndi Baala-zefoni.+ Ndipo anakamanga msasa pafupi ndi Migidoli.+ 8 Pambuyo pake ananyamuka ku Pihahiroti, n’kukadutsa panyanja+ kuwolokera kuchipululu.+ Anayendabe ulendo wa masiku atatu m’chipululu cha Etamu,+ n’kukamanga msasa ku Mara.+
9 Kenako ananyamuka ku Mara n’kukafika ku Elimu.+ Ku Elimuko anapezako akasupe 12 a madzi, ndi mitengo 70 ya kanjedza, ndipo anamanga msasa kumeneko. 10 Atanyamuka ku Elimu anakamanga msasa ku Nyanja Yofiira. 11 Atanyamuka ku Nyanja Yofiira anakamanga msasa m’chipululu cha Sini.+ 12 Kenako ananyamuka m’chipululu cha Sini, n’kukamanga msasa ku Dofika. 13 Atanyamuka ku Dofika anakamanga msasa ku Alusi. 14 Atanyamuka ku Alusi anakamanga msasa ku Refidimu.+ Kumeneko kunalibe madzi oti anthu amwe. 15 Atanyamuka ku Refidimu anakamanga msasa m’chipululu cha Sinai.+
16 Pambuyo pake ananyamuka m’chipululu cha Sinai, n’kukamanga msasa ku Kibiroti-hatava.+ 17 Atanyamuka ku Kibiroti-hatava, anakamanga msasa ku Hazeroti.+ 18 Pambuyo pake ananyamuka ku Hazeroti, n’kukamanga msasa ku Ritima. 19 Atanyamuka ku Ritima anakamanga msasa ku Rimoni-perezi. 20 Atanyamuka ku Rimoni-perezi anakamanga msasa ku Libina. 21 Pambuyo pake ananyamukanso ku Libina, n’kukamanga msasa ku Risa. 22 Kenako ananyamuka ku Risa n’kukamanga msasa ku Kehelata. 23 Atanyamuka ku Kehelata anakamanga msasa kuphiri la Saferi.
24 Pambuyo pake ananyamukanso kuphiri la Saferi, n’kukamanga msasa+ ku Harada. 25 Atanyamuka ku Harada anakamanga msasa ku Makeloti. 26 Atanyamuka+ ku Makeloti anakamanga msasa ku Tahati. 27 Atanyamuka ku Tahati anakamanga msasa ku Tera. 28 Kenako ananyamukanso ku Tera n’kukamanga msasa ku Mitika. 29 Atanyamuka ku Mitika anakamanga msasa ku Hasimona. 30 Atanyamuka ku Hasimona anakamanga msasa ku Mosera. 31 Kenako ananyamukanso ku Mosera n’kukamanga msasa ku Bene-yaakana.+ 32 Atanyamuka ku Bene-yaakana anakamanga msasa ku Hori-hagidigadi. 33 Atanyamuka ku Hori-hagidigadi anakamanga msasa ku Yotibata.+ 34 Pambuyo pake ananyamukanso ku Yotibata n’kukamanga msasa ku Abirona. 35 Kenako ananyamuka ku Abirona n’kukamanga msasa ku Ezioni-geberi.+ 36 Atanyamuka ku Ezioni-geberi anakamanga msasa m’chipululu cha Zini,+ ku Kadesi.
37 Pambuyo pake ananyamuka ku Kadesi, n’kukamanga msasa kuphiri la Hora,+ kumalire ndi dziko la Edomu. 38 Wansembe Aroni anakwera m’phiri la Hora monga mmene Yehova anamulamulira, ndipo anamwalira ali m’phirimo. Anamwalira m’chaka cha 40 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachisanu, pa tsiku loyamba la mweziwo.+ 39 Aroni anamwalira m’phiri la Hora ali ndi zaka 123.
40 Tsopano mfumu ina yachikanani, mfumu ya Aradi,+ imene inali kukhala ku Negebu+ m’dziko la kanani, inamva kuti ana a Isiraeli akubwera.
41 Patapita nthawi, Aisiraeliwo ananyamuka kuphiri la Hora,+ n’kukamanga msasa ku Tsalimona. 42 Pambuyo pake ananyamuka ku Tsalimona, n’kukamanga msasa ku Punoni. 43 Kenako ananyamukanso ku Punoni n’kukamanga msasa ku Oboti.+ 44 Atanyamuka ku Oboti anakamanga msasa ku Iye-abarimu,* kumalire ndi Mowabu.+ 45 Atanyamuka ku Iyimu anakamanga msasa ku Diboni-gadi.+ 46 Atanyamuka ku Diboni-gadi, anakamanga msasa ku Alimoni-dibilataimu. 47 Kenako ananyamukanso ku Alimoni-dibilataimu,+ n’kukamanga msasa kumapiri a Abarimu,+ pafupi ndi Nebo.+ 48 Potsirizira pake ananyamuka kumapiri a Abarimu n’kukamanga msasa ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+ 49 Anakhalabe mumsasa wawo pafupi ndi Yorodano, kuyambira ku Beti-yesimoti+ mpaka ku Abele-sitimu,+ m’chipululu cha Mowabu.
50 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose ku Yeriko, pafupi ndi Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+ Anamuuza kuti: 51 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Tsopano muwoloka Yorodano kuti mulowe m’dziko la Kanani.+ 52 Mukapitikitse anthu onse a m’dzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala,+ ndi mafano awo onse achitsulo.+ Mukawonongenso malo awo onse opatulika olambirira.+ 53 Mukalande dzikolo n’kukhalamo, chifukwa ndidzalipereka ndithu kwa inu kuti likhale lanu.+ 54 Mukagawire dzikolo kwa mabanja anu monga cholowa chanu mwa kuchita maere.+ Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo.+ Malo alionse amene maere akagwere banja, akapatsidwe kwa banjalo.+ Mukagawane malowo potsata mafuko a makolo anu.+
55 “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+ 56 Zikadzatero, zimene ndinafuna kuchita kwa anthuwo ndidzachita kwa inu.’”+
34 Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 2 “Lamula ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Pamene mukukalowa m’dziko la Kanani,+ nawa malire a dziko+ limene mudzalandire ngati cholowa chanu.+
3 “‘Chigawo chanu chakum’mwera chiyenera kuyambira kuchipululu cha Zini, kumalire a Edomu.+ Malire anu a kum’mwera ayenera kuchokera kumathero a Nyanja Yamchere,+ kum’mawa. 4 Malirewo akadutse kum’mwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, n’kuloweranso kum’mwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ n’kukafika ku Azimoni. 5 Ndiyeno malirewo akalowere kuchigwa* cha Iguputo+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu.+
6 “‘Malire anu a kumadzulo+ akatsatire gombe la Nyanja Yaikulu.
7 “‘Malire anu a kumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+ 8 Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo akafike ku Hamati,+ mpaka ku Zedadi.+ 9 Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka ku Hazara-enani.+ Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 “‘Ndiyeno mukalembe malire anu a kum’mawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu. 11 Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kum’mawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akagunde malo otsetsereka a kum’mawa kwa nyanja ya Kinereti.*+ 12 Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndilo dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’”
13 Chotero Mose anauza ana a Isiraeli kuti: “Ili ndilo dziko limene ligawidwe kwa inu mwa maere+ monga cholowa chanu. Lidzagawidwa kwa inu monga momwe Yehova analamulira kuti lipatsidwe kwa mafuko 9 ndi hafu.+ 14 Fuko la ana a Rubeni mwa mabanja a makolo awo, ndi fuko la ana a Gadi mwa mabanja a makolo awo, alandira kale cholowa chawo. Ndiponso hafu ya fuko la Manase, nawonso alandira kale cholowa chawo.+ 15 Mafuko awiri ndi hafuwo alandira kale cholowa chawo kudera la kum’mawa kwa Yorodano, moyang’anana ndi Yeriko.”+
16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 17 “Amuna amene akakugawireni malo monga cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa mwana wa Nuni.+ 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse, kuti akathandize kugawa cholowa cha malo.+ 19 Amunawo mayina awo ndi awa: Pa fuko la Yuda,+ Kalebe mwana wa Yefune, + 20 pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi, 21 pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni, 22 pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili, 23 pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi, 24 pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana, 25 pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki, 26 pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani, 27 pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi, 28 ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.” 29 Amenewa ndiwo amuna amene Yehova analamula kuti akagawire malo ana a Isiraeli, kuti akakhale ndi malo awoawo m’dziko la Kanani.+
35 Yehova analankhula ndi Mose m’chipululu cha Mowabu ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano,+ kuti: 2 “Lamula ana a Isiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapatseko Alevi mizinda+ yokhalamo. Akaperekenso kwa Aleviwo malo onse odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+ 3 Aleviwo azikakhala m’mizindayo, ndipo malo odyetserako ziwetowo akakhala a ziweto zawo, katundu wawo ndi nyama zawo zonse. 4 Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapatse Aleviwo, akakhale mikono 1,000 kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse. 5 Mukayeze kunja kwa mzinda, mikono 2,000 kumbali yakum’mawa, mikono 2,000 kumbali yakum’mwera, mikono 2,000 kumbali yakumadzulo, ndi mikono 2,000 kumbali yakumpoto, kuzungulira mzinda. Amenewa akakhale malo odyetserako ziweto kwa anthu a m’mizindayo.
6 “Mukapatse Alevi mizinda 6 yoti munthu amene wapha mnzake azikathawirako.+ Kuwonjezera pa mizindayi, mukapatse Aleviwo mizinda ina 42. 7 Mizinda yonse imene mukapatse Alevi ikakwane 48. Mizindayi mukawapatse limodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 8 Mizinda imene mukawapatseyo ikachokere kwa ana a Isiraeli.+ Fuko limene likakhale ndi mizinda yambiri mukatengeko yambiri, ndipo fuko limene likakhale ndi mizinda yochepa mukatengeko yochepa.+ Fuko lililonse likapereke ina ya mizinda yake kwa Alevi malinga ndi cholowa chawo chimene akalandire.”
9 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 10 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Muwoloka Yorodano kupita kudziko la Kanani.+ 11 Mukasankhe mizinda yoyenerera kwa inu, kuti ikakhale mizinda yanu yothawirako. Munthu amene wapha mnzake mwangozi azikathawira kumeneko.+ 12 Mizindayo ikakhale kothawirako munthu wopha mnzake amene akuthawa wobwezera magazi,+ kuti amene wapha mnzakeyo asaphedwe kufikira ataima pamaso pa oweruza kuti aweruzidwe.+ 13 Ndipo mizinda imene mukaperekeyo, mizinda yothawirako 6 imeneyo, izikagwira ntchito imeneyi. 14 Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yorodano,+ ndiponso mukapereke mizinda itatu tsidya linalo, m’dziko la Kanani.+ Imeneyi ikakhala mizinda yothawirako. 15 Kwa ana a Isiraeli, kwa mlendo,+ ndi kwa munthu amene wakhaliratu pakati pawo, mizinda 6 imeneyi ikakhala kothawirako aliyense amene wapha munthu mwangozi.+
16 “‘Ngati munthu wamenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo n’kufa, ameneyo ndi wakupha munthu.+ Ndipo wakupha munthuyo ayenera kuphedwa ndithu.+ 17 Ngati walasa mnzake ndi mwala umene ungamuphe, mnzakeyo n’kufadi, ameneyo ndi wakupha munthu. Ndipo wakupha munthuyo aphedwe ndithu. 18 Ngati wamenya mnzake ndi mtengo umene ungamuphe, mnzakeyo n’kufadi, ameneyo ndi wakupha munthu. Ndipo wakupha munthuyo aphedwe ndithu.
19 “‘Wobwezera magazi+ ndi amene ayenera kupha wakupha munthuyo. Akadzangom’peza, wobwezera magaziyo adzamuphe. 20 Ndipo ngati chifukwa chodana naye anamukankha,+ kapena ngati anamulasa ndi chinthu atamubisalira,+ mnzakeyo n’kufa, 21 kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+
22 “‘Koma ngati wamukankha mwangozi, osati chifukwa cha chidani, kapena ngati wam’ponyera chinachake mwangozi, osati mochita kum’bisalira,+ 23 kapena ngati mosaona wamulasa ndi mwala umene ungamuphe, kapena kumugwetsera mwalawo, mnzakeyo n’kufa, koma sanali naye chidani chilichonse, kapena cholinga chofuna kumuvulaza, 24 oweruza aweruze pakati pa wopha mnzakeyo ndi woyenera kubwezera magaziyo, malinga ndi malamulo amenewa.+ 25 Oweruzawo+ alanditse wakupha munthuyo m’manja mwa wobwezera magazi, ndipo am’bwezere kumzinda wothawirako kumene anathawira. Iye ayenera kukhala mumzindamo mpaka mkulu wa ansembe amene anadzozedwa ndi mafuta opatulika+ adzamwalire.
26 “‘Koma wopha munthuyo akatuluka kunja kwa malire a mzinda wothawirako kumene anathawira, 27 wobwezera magazi+ n’kumupeza kunja kwa malire a mzinda wothawirako, n’kumupha, wobwezera magaziyo alibe mlandu wa magazi. 28 Wakupha munthuyo ayenera kukhala mumzinda wothawirako kufikira mkulu wa ansembe atamwalira.+ Pambuyo pa imfa ya mkulu wa ansembe, wakupha munthuyo ayenera kubwerera kumalo a cholowa chake. 29 Amenewa akhale malamulo anu oweruzira milandu m’mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.
30 “‘Aliyense wopezeka kuti wapha munthu,+ atatsimikiziridwa ndi mboni,+ aphedwe. Koma umboni wa munthu mmodzi si wokwanira kuti munthu aphedwe. 31 Ndipo musalandire dipo lowombolera moyo wa munthu wakupha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa.+ Aphedwe ndithu ameneyo.+ 32 Komanso musalandire dipo loperekedwa ndi cholinga chofuna kuwombola munthu amene anathawira kumzinda wothawirako kuti abwerere kwawo mkulu wa ansembe asanamwalire.
33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ 34 Musaipitse dziko limene mukukhalamo, limene inenso ndikukhalamo, pakuti ine Yehova ndikukhala pakati pa ana a Isiraeli.’”+
36 Atsogoleri a mabanja a ana a Giliyadi mwana wa Makiri,+ mwana wa Manase, ochokera kumabanja a ana a Yosefe, anafika ndi kulankhula ndi Mose ndi akalonga omwe anali atsogoleri a ana a Isiraeli. 2 Iwo anati: “Paja Yehova anakulamulani inu mbuyathu, kuti mugawire dzikoli ana a Isiraeli monga cholowa chawo, mwa kuchita maere.+ Yehova anakulamulaninso kuti cholowa cha m’bale wathu Tselofekadi muchipereke kwa ana ake aakazi.+ 3 Tsopano ana aakaziwa akadzakwatiwa ndi amuna a mafuko ena a ana a Isiraeli, ndiye kuti cholowa chawo chidzachotsedwa ku cholowa cha makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense adzakwatiweko. Zikadzatero ndiye kuti cholowa chathu cha malo chidzachepa.+ 4 Chaka cha Ufulu+ cha ana a Isiraeli chikadzafika, cholowa cha akaziwa chidzachotsedwa ku cholowa cha fuko la makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense wa iwo adzakwatiweko ndipo chidzakhala cha fukolo mpaka kalekale.”
5 Pamenepo Mose anauza ana a Isiraeli zimene Yehova anamuuza, kuti: “Fuko la ana a Yosefe likunena zoona. 6 Zimene Yehova walamula zokhudza ana aakazi a Tselofekadi+ n’zakuti, ‘Iwo angakwatiwe ndi aliyense amene wawakomera m’maso. Koma akwatiwe ndi amuna a fuko la makolo awo okha.+ 7 Cholowa cha ana a Isiraeli chisachoke ku fuko lina kupita ku fuko lina. Aliyense wa ana a Isiraeli ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. 8 Choncho, mwana wamkazi aliyense amene walandira nawo cholowa pakati pa mafuko a ana a Isiraeli, azikwatiwa ndi mwamuna wa m’banja la fuko la bambo ake,+ kuti aliyense wa ana a Isiraeli azilandira cholowa chochokera kwa makolo ake. 9 Cholowa chilichonse chisachoke ku fuko lina kupita ku fuko lina. Fuko lililonse la ana a Isiraeli lizisunga cholowa chake.’”
10 Ana aakazi a Tselofekadi amenewo anachitadi zimene Yehova analamula Mose.+ 11 Chotero, Mala, Tiriza, Hogila, Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Tselofekadi,+ anakwatiwa ndi ana a abale* a bambo awo. 12 Anakwatiwa ku mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, kuti cholowa chawo chisachoke ku fuko la banja la bambo awo.
13 Amenewa ndiwo malamulo+ ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa ana a Isiraeli kudzera kwa Mose ku Yeriko, m’chipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:5.
Mawu ake enieni, “tulutsa umuna.”
“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Nu 5:13.
Mawu akuti “ntchafu,” mwina akuimira maliseche.
Kapena kuti “Ame! Ame!” m’Chiheberi.
“Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinali kupangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Dzina limeneli limatanthauza “Kuyaka; Moto Walawilawi.”
Mawu ake enieni, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.
Ena amati “kunzuna.”
“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.
Kapena kuti “Yoswa,” kutanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.”
Kapena kuti “Chiphona.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Mawu akuti “Anefili” amatanthauza “ogwetsa anzawo.”
Mawu ake enieni, “dama.”
Gawo limodzi la magawo 10 a muyezo wotchedwa “efa” ndi lofanana ndi malita awiri.
“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.
Onani Zakumapeto 5.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Mawu ake enieni, “pangano la mchere.”
Mawu ake enieni pa mawu akuti “chosavundikira bwino,” ndi akuti “chosamanga chingwe chake.”
Dzina lakuti “Meriba” limatanthauza “Kukangana; Kutsutsana; Kulimbana.”
Dzina lakuti “Horima” limatanthauza “chinthu choperekedwa kuti chiwonongedwe kotheratu.”
Kapena kuti “njoka yamoto.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Buluyu anali wamkazi.
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Onani mawu a m’munsi pa Nu 23:22.
“Kayini” akuimira fuko la “Akeni.”
Ena amati “kugwaza.”
“Azichimwene” akutanthauza abale a munthu aamuna, obadwa kwa mayi ndi bambo mmodzi.
Mawu ake enieni, “munthu amene mwa iye muli mzimu.”
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
“Kudzisautsa” pano kungatanthauze kusala chakudya ndiponso kutsatira malamulo ena ofanana ndi kuchita zimenezi.
Ena amati “masikiyo.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake enieni, “dzanja lokwezeka.”
Dzina lakuti “Iye-abarimu” lalembedwa mwachidule kuti “Iyimu” m’vesi 45.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
M’Baibulo, “nyanja ya Kinereti” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Genesarete,” “nyanja ya Galileya” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”
“Abale a bambo awo” akutanthauza akulu awo kapena ang’ono awo a bambo awo.