LEVITIKO
1 Yehova anaitana Mose kuchokera mʼchihema chokumanako,+ nʼkumuuza kuti: 2 “Uza Aisiraeli* kuti, ‘Ngati munthu aliyense akufuna kupereka chiweto kwa Yehova kuti ikhale nsembe, azipereka ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.+
3 Ngati akupereka ngʼombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako. 4 Iye aziika dzanja lake pamutu pa nsembe yopserezayo ndipo idzalandiridwa kuti iphimbe machimo ake.
5 Kenako azipha ngʼombe yaingʼono pamaso pa Yehova. Ndiyeno ana a Aroni ansembe,+ azibweretsa magazi ake nʼkuwawaza mbali zonse za guwa lansembe,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako. 6 Nyama ya nsembe yopserezayo aziisenda nʼkuiduladula.+ 7 Ana a Aroni, ansembe, aziika moto paguwa lansembelo+ nʼkuyalapo nkhuni. 8 Ndiyeno ana a Aroni ansembe, aziyala nyama yoduladulayo+ pankhuni zimene zili pamoto wapaguwa lansembepo. Aziyala nyamayo pamodzi ndi mutu ndiponso mafuta.* 9 Matumbo ake ndi ziboda zake azizitsuka ndi madzi. Akatero wansembe aziwotcha nyama yonse kuti paguwa lansembe pakhale utsi, ndipo ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+
10 Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi+ kuti ikhale nsembe yake yopsereza, azipereka mwana wamphongo wopanda chilema.+ 11 Ndipo aziipha pamaso pa Yehova kumbali yakumpoto ya guwa lansembe. Akatero ana a Aroni ansembe, aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe.+ 12 Kenako nyamayo aziiduladula ndipo azichotsa mafuta ake* ndi mutu wake. Akatero wansembe aziyala nyama yoduladulayo pankhuni zimene zili pamoto wapaguwa lansembe. 13 Ndiyeno azitsuka matumbo komanso ziboda ndi madzi. Kenako wansembe aziwotcha nyama yonse kuti paguwa lansembe pakhale utsi, ndipo ikhale nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.
14 Koma ngati akupereka mbalame kuti ikhale nsembe yake yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, azipereka njiwa kapena ana a nkhunda.+ 15 Wansembe azibweretsa mbalameyo paguwa lansembe nʼkudula* mutu wake. Akatero aziiwotcha paguwa lansembe kuti pakhale utsi, koma magazi ake aziwakhetsera pansi pambali pa guwa lansembelo. 16 Azichotsa chithokomiro ndi nthenga zake nʼkuziponya potayira phulusa,*+ chakumʼmawa, pafupi ndi guwa lansembe. 17 Ndiyeno aziingʼamba pakati chamʼmapiko mwake, koma osailekanitsa. Kenako wansembe aziiwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nkhuni zimene zili pamoto kuti pakhale utsi. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.’”
2 “‘Ngati munthu akupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, azipereka ufa wosalala. Azithira mafuta nʼkuika lubani* pa ufawo.+ 2 Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, nʼkuuwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova. 3 Ndipo zotsala pa nsembe yambewu zizikhala za Aroni ndi ana ake,+ chifukwa ndi zopatulika koposa,+ zochokera pansembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova.
4 Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati, wopanda zofufumitsa, wothira mafuta. Kapena muzipereka timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+
5 Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mʼchiwaya,+ izikhala ya ufa wabwino kwambiri wothira mafuta, yopanda zofufumitsa. 6 Muziibenthula zidutswazidutswa nʼkuithira mafuta.+ Imeneyi ndi nsembe yambewu.
7 Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mʼchiwaya, izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala ndiponso mafuta. 8 Nsembe yambewu imene yapangidwa ndi zinthu zimenezi muzibwera nayo kwa Yehova. Muziipereka kwa wansembe ndipo iye azipita nayo paguwa lansembe. 9 Kenako wansembe azitengako pangʼono nsembe yambewu kuimira nsembe yonseyo,+ ndipo aziwotcha zimene watengazo paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+ 10 Ndipo zimene zatsala pansembe yambewu zizikhala za Aroni ndi ana ake, chifukwa ndi zopatulika koposa zochokera pansembe zowotcha pamoto+ zoperekedwa kwa Yehova.
11 Nsembe yambewu imene mukupereka kwa Yehova isakhale ndi zofufumitsa,+ chifukwa simukuyenera kuwotcha ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa kapena uchi,* ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
12 Zimenezi mungathe kuzipereka kwa Yehova ngati nsembe ya zipatso zoyambirira,+ koma simukuyenera kuzibweretsa paguwa lansembe kuti zikhale nsembe yakafungo kosangalatsa.*
13 Nsembe yanu iliyonse yambewu muziithira mchere. Popereka nsembe yambewu musamaiwale kupereka mchere wokukumbutsani pangano la Mulungu. Mukamapereka nsembe iliyonse, muziperekanso mchere.+
14 Mukamapereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha, muzipereka tirigu watsopano* wokazinga pamoto, wosinja kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha.+ 15 Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu. 16 Wansembe aziwotcha zinthu zimenezi kuimira nsembe yonseyo,+ zomwe ndi wina mwa tirigu wosinja uja komanso mafuta, pamodzi ndi lubani wake yense, kuti zikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.’”
3 “‘Ngati akupereka nsembe yamgwirizano*+ kwa Yehova ndipo akufuna kupereka ngʼombe yamphongo kapena yaikazi, azipereka yopanda chilema. 2 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo iziphedwa pakhomo la chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni ansembe, aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 3 Azipereka mbali ina ya nsembe yamgwirizanoyo ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ Azipereka mafuta+ okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo. 4 Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo omwe ali pafupi ndi chiuno. Koma mafuta apachiwindi aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+ 5 Kenako ana a Aroni aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe, pamwamba pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni zimene zili pamoto.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+
6 Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yamgwirizano kwa Yehova, azipereka yamphongo kapena yaikazi, yopanda chilema.+ 7 Ngati akupereka nkhosa yaingʼono yamphongo monga nsembe yake, aziibweretsa kwa Yehova. 8 Kenako aziika dzanja lake pamutu pa nkhosayo ndipo iziphedwa patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 9 Ndipo pansembe yamgwirizanoyo azitengapo mafuta ake ndi kuwapereka kwa Yehova+ monga nsembe yowotcha pamoto. Azichotsa mchira wonse wamafuta pafupi ndi fupa la msana ndiponso mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo. 10 Azichotsanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 11 Ndipo wansembe aziwotcha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya,* kuti zikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+
12 Ngati akupereka mbuzi monga nsembe yake, aziibweretsa pamaso pa Yehova. 13 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo iziphedwa patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni aziwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 14 Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo,+ nʼkuwapereka kwa Yehova ngati nsembe yowotcha pamoto. 15 Aziperekanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo. 16 Wansembe aziwotcha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya.* Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa.* Mafuta onse ndi a Yehova.+
17 Musamadye mafuta kapena magazi alionse.+ Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kulikonse kumene mungakhale.’”
4 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa+ pochita zinthu zimene Yehova analamula kuti musachite, muzichita izi:
3 Ngati wansembe wodzozedwa+ wachita tchimo+ ndipo lapangitsa anthu onse kupalamula, azipereka kwa Yehova ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+ 4 Azibweretsa ngʼombe yamphongoyo pamaso pa Yehova pakhomo la chihema chokumanako+ ndipo aziika dzanja lake pamutu wa ngʼombeyo, kenako aziipha pamaso pa Yehova.+ 5 Ndiyeno wansembe wodzozedwayo,+ azitengako pangʼono magazi a ngʼombeyo nʼkulowa nawo mʼchihema chokumanako. 6 Kenako wansembe aziviika chala chake mʼmagaziwo+ nʼkudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7+ pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani ya malo oyera. 7 Wansembeyo azipakanso ena mwa magaziwo panyanga za guwa lansembe la zofukiza zonunkhira,+ limene lili pamaso pa Yehova mʼchihema chokumanako. Magazi ena onse a ngʼombeyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako.
8 Kenako azichotsa mafuta onse a ngʼombe ya nsembe yamachimo, kuphatikizapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse apamatumbo. 9 Azichotsanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 10 Zinthu zimenezi zizikhala zofanana ndi zomwe azichotsa pa ngʼombe ya nsembe yamgwirizano.+ Ndipo wansembe aziziwotcha paguwa lansembe zopsereza.
11 Koma kunena za chikopa cha ngʼombeyo ndi nyama yake yonse pamodzi ndi mutu wake, ziboda zake, matumbo ake ndi ndowe zake,+ 12 kutanthauza ngʼombe yonseyo, aziitenga nʼkupita nayo kunja kwa msasa. Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa* ndipo aziiwotcha pamoto+ wa nkhuni. Aziwotcha ngʼombeyo kumalo otayako phulusa.
13 Tsopano ngati gulu lonse la Isiraeli lapalamula pochita tchimo mosadziwa,+ koma mpingo* sunazindikire kuti iwo achita zimene Yehova anawalamula kuti asachite,+ 14 ndipo kenako tchimolo ladziwika, mpingowo uzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo, ndipo azibwera nayo pakhomo la chihema chokumanako. 15 Akulu a gulu la Isiraeli aziika manja awo pamutu wa ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo iziphedwa pamaso pa Yehova.
16 Kenako wansembe wodzozedwa, azibweretsa ena mwa magazi a ngʼombeyo mʼchihema chokumanako. 17 Wansembe aziviika chala chake mʼmagaziwo nʼkudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7 pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani.+ 18 Kenako azipaka ena mwa magaziwo panyanga za guwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova, mʼchihema chokumanako. Magazi ena onse aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pakhomo la chihema chokumanako.+ 19 Akatero azichotsa mafuta ake onse ndi kuwawotcha paguwa lansembe.+ 20 Ngʼombeyo azichita nayo ngati mmene anachitira ndi ngʼombe ina ya nsembe yamachimo ija. Azichita zomwezo, ndipo wansembe aziwaphimbira machimo awo+ ndipo adzakhululukidwa. 21 Azitenga ngʼombeyo nʼkupita nayo kunja kwa msasa ndipo aziiwotcha ngati mmene anawotchera ngʼombe yoyamba ija.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo ya mpingo wonse.+
22 Ngati mtsogoleri+ wachimwa mosadziwa pochita chimodzi mwa zinthu zonse zimene Yehova Mulungu wake analamula kuti asachite ndipo wapalamula, 23 kapena ngati wadziwa kuti wachimwa pochita zinthu zosemphana ndi lamulo, azibweretsa mbuzi yaingʼono yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yake. 24 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa mbuzi yaingʼonoyo ndipo aziipha pamaso pa Yehova,+ pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 25 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimoyo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza.+ 26 Mafuta onse a mbuziyo aziwawotcha paguwa lansembe mofanana ndi mafuta a nsembe yamgwirizano.+ Pamenepo wansembe aziphimba tchimo la mtsogoleriyo, ndipo adzakhululukidwa.
27 Ngati munthu aliyense pakati panu wachimwa mosazindikira pochita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite+ ndipo wapalamula, 28 kapena ngati wadziwa kuti wachimwa, azibweretsa mbuzi yaingʼono yaikazi, yopanda chilema kuti ikhale nsembe chifukwa cha tchimo lakelo. 29 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo azipha nyamayo pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza aja.+ 30 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza.+ 31 Kenako azichotsa mafuta onse a mbuziyo,+ ngati mmene amachotsera mafuta a nsembe yamgwirizano.+ Akatero wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe kuti akhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.
32 Koma ngati akupereka nkhosa monga nsembe yake yamachimo, azibweretsa nkhosa yaingʼono yaikazi yopanda chilema. 33 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo aziipha kuti ikhale nsembe yamachimo, pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza.+ 34 Wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza.+ Magazi ena onse a nkhosayo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 35 Ndiyeno azichotsa mafuta onse a nkhosayo, monga mmene amachotsera mafuta a nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yamgwirizano. Akatero wansembe aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova.+ Wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita, ndipo adzakhululukidwa.’”+
5 “‘Munthu akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo kuti akachitire umboni+ za tchimolo* koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.
2 Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire, iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu. 3 Kapena munthu akakhudza mosadziwa chodetsa chilichonse chochokera kwa munthu,+ kutanthauza chinthu chilichonse chodetsedwa chimene chingamuchititse kuti akhale wodetsedwa ndipo wadziwa zimenezi, ndiye kuti wapalamula mlandu.
4 Kapenanso munthu akafulumira kulumbira kuti achita chinachake, kaya chabwino kapena choipa koma sanazindikire, kenako nʼkuzindikira kuti analumbira mofulumira, ndiye kuti wapalamula mlandu.*+
5 Akapalamula mlandu wokhudzana ndi chimodzi mwa zinthu zimenezi, aziulula tchimo+ limene wachita. 6 Azibweretsanso kwa Yehova nsembe yake yakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita.+ Azibweretsa nkhosa yaingʼono yaikazi kapena mbuzi yaingʼono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.
7 Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa, azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ kuti zikhale nsembe zakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+ 8 Azibweretsa mbalamezi kwa wansembe, ndipo wansembeyo azipereka nsembe yamachimo choyamba, ataicheka pakhosi koma osaduliratu mutu wake. 9 Kenako azidontheza ena mwa magazi a nsembe yamachimo mʼmbali mwa guwa lansembe, koma magazi otsalawo aziwathira pansi pa guwa lansembelo.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Mbalame inayo aziipereka ngati nsembe yopsereza motsatira ndondomeko ya nthawi zonse.+ Choncho wansembe aziphimba machimo amene munthuyo wachita, ndipo adzakhululukidwa.+
11 Koma ngati sangakwanitse kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ kuti ukhale nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lake. Asauthire mafuta ndipo asaikemo lubani chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo. 12 Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuimira nsembe yonseyo. Kenako auwotche paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 13 Wansembeyo aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Aziphimba tchimo lililonse mwa machimo amenewa ndipo adzakhululukidwa.+ Zinthu zimene zatsala pa nsembeyo zizikhala za wansembe+ mofanana ndi nsembe yambewu.’”+
14 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 15 “Munthu akachita mosakhulupirika pochimwira zinthu zopatulika kwa Yehova mosadziwa,+ azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake yakupalamula.+ Potchula mtengo wa nkhosayo azigwiritsa ntchito masekeli* asiliva ofanana ndi sekeli lakumalo oyera.*+ 16 Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera, azilipira ndipo aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Malipirowo aziwapereka kwa wansembe limodzi ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula, kenako wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo adzakhululukidwa.+
17 Munthu akachimwa pochita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira, wapalamulabe mlandu ndipo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ 18 Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe yakupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene anachita mosadziwa ndipo adzakhululukidwa. 19 Imeneyi ndi nsembe yakupalamula. Munthu ameneyo wapalamula mlandu chifukwa wachimwira Yehova.”
6 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: 2 “Munthu akachimwa ndipo wachita mosakhulupirika kwa Yehova+ ponamiza mnzake pa chinthu chimene anamusungitsa,+ kapena chimene anamubwereka, kapena wamubera mnzake, kapena wamuchitira chinyengo, 3 kapena watola chinthu chotayika koma akukana kuti sanachitole, ndipo ngati walumbira monama pa tchimo lililonse limene angachite,+ azichita izi: 4 Ngati wachimwa ndipo wapalamula mlandu, azibweza zinthu zimene anabazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene anamʼsungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola, 5 kapena chilichonse chimene analumbira monama. Azibweza chinthucho+ nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake 5. Azibweza zimenezi kwa mwiniwake pa tsiku limene wapezeka kuti ndi wolakwa. 6 Ndipo azibweretsa kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake yakupalamula, yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi mtengo umene wagamulidwa kuti ikhale nsembe yakupalamula.+ 7 Wansembe aziphimba machimo a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chimene wachita chimene chapangitsa kuti apalamule mlandu.”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 9 “Lamula Aroni ndi ana ake kuti, ‘Ili ndi lamulo la nsembe yopsereza:+ Nsembe yopsereza izikhala pamoto, paguwa lansembe, usiku wonse mpaka mʼmawa ndipo moto wapaguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Wansembe azivala zovala zake zogwirira ntchito+ komanso azivala kabudula wansalu+ wobisa* thupi lake. Kenako azichotsa phulusa*+ la nsembe yopsereza imene yawotchedwa pamoto wapaguwalo ndipo aziika phulusalo pambali pa guwa lansembe. 11 Ndiyeno azivula zovalazo+ nʼkuvala zina. Akatero azitenga phulusalo nʼkupita nalo kumalo oyera, kunja kwa msasa.+ 12 Moto wapaguwa lansembe uziyaka nthawi zonse. Usamazime. Wansembe aziikapo nkhuni+ mʼmawa uliwonse nʼkuikapo nsembe yopsereza. Akatero aziwotcha mafuta a nsembe yamgwirizano pamotopo.+ 13 Motowo uziyaka nthawi zonse paguwa lansembe. Usamazime.
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi komanso azitengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, aziziwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda zofufumitsa ndi kudya mkatewo mʼmalo oyera. Aziudyera mʼbwalo la chihema chokumanako.+ 17 Pophika, musaikemo zofufumitsa zilizonse.+ Ndaupereka monga gawo lawo kuchokera pansembe zanga zowotcha pamoto.+ Zimenezi nʼzopatulika koposa+ mofanana ndi nsembe yamachimo komanso nsembe yakupalamula. 18 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni azidya mkatewo.+ Limeneli ndi gawo lawo lochokera pansembe zowotcha pamoto+ zoperekedwa kwa Yehova, mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale. Chilichonse chimene chingakhudze nsembezi chidzakhala choyera.’”
19 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 20 “Iyi ndi nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene akudzozedwa:+ ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ uzikhala nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse. Hafu ya ufawo azipereka mʼmamawa ndipo hafu inayo madzulo. 21 Nsembeyo izikhala yophika ndi mafuta mʼchiwaya.+ Izikhala yosakaniza bwino ndi mafuta. Uzipereka mitanda yophika ya nsembe yambewu monga kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 22 Wansembe wodzozedwa amene adzalowe mʼmalo mwake, kuchokera pakati pa ana ake,+ azipereka nsembeyo. Aziwotcha nsembe yonseyo kuti ikhale nsembe yoperekedwa kwa Yehova. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 23 Nsembe iliyonse yambewu ya wansembe iziwotchedwa yonse. Sikuyenera kudyedwa.”
24 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 25 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Ili ndi lamulo la nsembe yamachimo:+ Pamalo amene mukuphera nyama ya nsembe yopsereza+ muzipheraponso nyama ya nsembe yamachimo pamaso pa Yehova. Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 26 Wansembe amene waipereka monga nsembe yamachimo aziidya.+ Aziidyera kumalo oyera, mʼbwalo la chihema chokumanako.+
27 Chilichonse chimene chingakhudze mnofu wake chidzakhala choyera, ndipo ngati munthu wadonthezera ena mwa magazi a nyamayo pachovala, chovala chimene wadonthezera magazicho muzichichapira kumalo oyera. 28 Ndipo chiwiya chadothi chimene mungawiritsiremo nyamayo muzichiswa. Koma mukawiritsira mʼchiwiya chakopa,* muzichikwecha nʼkuchitsuka ndi madzi.
29 Mwamuna aliyense amene ndi wansembe azidya nyamayo.+ Ndi yopatulika koposa.+ 30 Koma nyama ya nsembe yamachimo sikuyenera kudyedwa ngati ena mwa magazi ake analowa nawo mʼchihema chokumanako kuti aphimbire machimo mʼmalo oyera.+ Imeneyo muziiwotcha pamoto.’”
7 “‘Lamulo la nsembe yakupalamula+ ndi ili: Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 2 Nyama ya nsembe yakupalamula aziiphera pamalo amene amaphera nyama ya nsembe yopsereza, ndipo magazi ake+ aziwazidwa mbali zonse za guwa lansembe.+ 3 Azipereka mafuta ake onse,+ kuphatikizapo mchira wamafuta, mafuta okuta matumbo, 4 impso ziwiri zimene zili pafupi ndi chiuno komanso mafuta okuta impsozo. Azichotsanso mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 5 Wansembe aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe monga nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe yakupalamula. 6 Mwamuna aliyense yemwe ndi wansembe azidya nyamayo+ ndipo aziidyera mʼmalo oyera. Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+ 7 Lamulo la nsembe yakupalamula ndi lofanana ndi la nsembe yamachimo. Nyama ya nsembeyi izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo pophimba machimo.+
8 Wansembe akaperekera munthu nsembe yopsereza, chikopa+ cha nsembeyo chizikhala cha wansembe amene wapereka nsembeyo.
9 Nsembe iliyonse yambewu imene yaphikidwa mu uvuni kapena mʼchiwaya+ izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo. Izikhala yake.+ 10 Koma nsembe yambewu iliyonse yothira mafuta+ kapena yosathira mafuta+ izikhala ya ana onse aamuna a Aroni, azigawana mofanana.
11 Tsopano lamulo la nsembe yamgwirizano+ imene aliyense azipereka kwa Yehova ndi ili: 12 Ngati akupereka nsembeyo posonyeza kuyamikira,+ azipereka nsembe yoyamikira pamodzi ndi mkate wozungulira woboola pakati, wopanda zofufumitsa, wothira mafuta. Aziperekanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta komanso mkate wozungulira woboola pakati, wothira mafuta, wophika ndi ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta. 13 Azipereka nsembe yake pamodzi ndi mitanda ya mkate yozungulira yoboola pakati, yokhala ndi zofufumitsa. Aziipereka pamodzi ndi nsembe zamgwirizano zimene akuzipereka posonyeza kuyamikira. 14 Pa zinthu zimenezi azipereka mtanda umodzi wa nsembe iliyonse kuti ikhale gawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova. Mtandawo uzikhala wa wansembe amene wawaza magazi a nsembe zamgwirizanozo paguwa lansembe.+ 15 Nyama ya nsembe zamgwirizano zimene zaperekedwa monga nsembe yoyamikira aziidya pa tsiku limene waipereka. Asasunge nyama iliyonse mpaka mʼmamawa.+
16 Ngati akupereka nsembe chifukwa cha lonjezo limene anapanga+ kapena ngati akupereka nsembe yaufulu,+ aziidya pa tsiku limene wapereka nsembeyo, ndipo yotsala angathenso kuidya pa tsiku lotsatira. 17 Koma ngati nyama ya nsembeyo yatsala mpaka tsiku lachitatu, ayenera kuiwotcha pamoto.+ 18 Koma ngati nyama iliyonse ya nsembe yamgwirizano yadyedwa pa tsiku lachitatu, wopereka nsembeyo Mulungu sadzasangalala naye. Nsembe yakeyo idzakhala yopanda phindu. Idzakhala chinthu chonyansa, ndipo amene wadya nsembeyo adzayankha mlandu chifukwa cha kulakwa kwake.+ 19 Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, siyenera kudyedwa. Muziiwotcha pamoto. Koma aliyense woyera angathe kudya nyama imene sinadetsedwe.
20 Munthu aliyense wodetsedwa amene wadya nyama ya nsembe yamgwirizano, imene ndi ya Yehova, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 21 Munthu akakhudza chilichonse chodetsedwa, kaya ndi chodetsa chochokera kwa munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ nʼkudya ina mwa nyama ya nsembe yamgwirizano, imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.’”
22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 23 “Uwauze Aisiraeli kuti, ‘Musamadye mafuta alionse+ a ngʼombe, a mwana wa nkhosa kapena a mbuzi. 24 Mafuta a nyama imene mwaipeza yakufa komanso mafuta a nyama imene yaphedwa ndi nyama inzake, mungathe kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma musamawadye ngakhale pangʼono.+ 25 Aliyense amene wadya mafuta a nyama imene waipereka kwa Yehova ngati nsembe yowotcha pamoto, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.
26 Musamadye magazi alionse+ kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama. 27 Munthu aliyense wodya magazi alionse aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.’”
28 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 29 “Uwauze Aisiraeli kuti, ‘Munthu amene akubweretsa nsembe yake yamgwirizano kwa Yehova,+ azipereka mbali ya nsembe yake yamgwirizanoyo kwa Yehova. 30 Iye azibweretsa yekha mafuta+ pamodzi ndi chidale ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. Ndipo aziyendetsa zinthu zimenezi uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku+ yoperekedwa kwa Yehova. 31 Wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe,+ koma chidalecho chizikhala cha Aroni ndi ana ake.+
32 Mwendo wakumbuyo wakumanja muziupereka kwa wansembe monga gawo lopatulika lochokera pansembe zanu zamgwirizano.+ 33 Mwana wa Aroni amene wapereka kwa Mulungu magazi a nsembe zamgwirizano ndiponso mafuta, azitenga mwendo wakumbuyo wakumanja monga gawo lake.+ 34 Ine ndikutenga chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndiponso mwendo womwe ndi gawo lopatulika. Ndikutenga zimenezi pansembe zamgwirizano za Aisiraeli nʼkuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli mpaka kalekale.+
35 Limeneli linali gawo la Aroni ndi ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa kuti atumikire monga ansembe a Yehova.+ 36 Yehova analamula kuti aziwapatsa gawoli kuchokera kwa Aisiraeli, pa tsiku limene anawadzoza.+ Limeneli ndi lamulo mʼmibadwo yawo yonse mpaka kalekale.’”
37 Limeneli ndi lamulo lokhudza nsembe yopsereza,+ nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo,+ nsembe yakupalamula,+ nyama yoperekedwa poika munthu kuti akhale wansembe+ ndiponso nsembe yamgwirizano,+ 38 mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose paphiri la Sinai,+ pa tsiku limene analamula Aisiraeli kuti azipereka nsembe zawo kwa Yehova mʼchipululu cha Sinai.+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Tenga Aroni limodzi ndi ana ake,+ zovala zawo,+ mafuta odzozera,+ ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi dengu la mikate yopanda zofufumitsa.+ 3 Ndiyeno usonkhanitse gulu lonse pakhomo la chihema chokumanako.”
4 Mose anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Ndipo gulu lonse linasonkhana pakhomo la chihema chokumanako. 5 Kenako Mose anauza gululo kuti: “Yehova walamula kuti tichite zinthu izi.” 6 Choncho Mose anaitana Aroni ndi ana ake nʼkuwasambitsa ndi madzi.+ 7 Atatero anaveka Aroni mkanjo+ nʼkumumanga lamba wapamimba.*+ Anamuvekanso malaya odula manja+ komanso efodi+ ndipo anamanga lamba woluka+ wa efodiyo. 8 Kenako anamuveka chovala chapachifuwa+ nʼkuika Urimu ndi Tumimu+ mʼchovala chapachifuwacho. 9 Anamuvekanso nduwira+ kumutu kwake, nʼkuika patsogolo pa nduwirayo kachitsulo konyezimira kagolide, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
10 Ndiyeno Mose anatenga mafuta odzozera nʼkudzoza chihema ndi zonse zimene zinali mkati mwake,+ kuti zikhale zopatulika. 11 Anawaza ena mwa mafuta odzozerawo maulendo 7 paguwa lansembe nʼkudzoza guwa lansembelo, zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake, kuti zikhale zopatulika. 12 Pomaliza Mose anathira ena mwa mafuta odzozera pamutu pa Aroni nʼkumudzoza kuti akhale wopatulika.+
13 Kenako Mose anaitana ana a Aroni ndipo anawaveka mikanjo, anawamanga malamba apamimba komanso anawakulunga mipango kumutu,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
14 Atatero anabweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa ngʼombe ya nsembe yamachimoyo.+ 15 Ndiyeno Mose anapha ngʼombeyo nʼkutenga magazi+ ndi chala chake ndipo anawapaka panyanga zonse za guwa lansembe nʼkuyeretsa guwalo ku uchimo. Koma magazi otsalawo anawathira pansi pa guwa lansembe kuti alipatule, kuphimba machimo paguwalo. 16 Atatero Mose anatenga mafuta onse okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake, nʼkuziwotcha paguwa lansembe.+ 17 Koma ngʼombe yonseyo, chikopa chake, nyama yake ndi ndowe zake anaziwotcha pamoto kunja kwa msasa,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
18 Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 19 Ndiyeno Mose anapha nkhosayo nʼkuwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 20 Anaduladula nkhosayo ndipo Mose anatenga mutu wake, nyama yoduladulayo ndi mafuta ake,* nʼkuziwotcha. 21 Anatsuka matumbo ndi ziboda ndipo Mose anawotcha paguwa lansembe nkhosa yonseyo. Inali nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa.* Komanso inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
22 Kenako anabweretsa nkhosa yamphongo yachiwiri, nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe,+ ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 23 Mose anapha nkhosayo ndi kutengako magazi ake nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la Aroni, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja. 24 Kenako Mose anaitana ana a Aroni nʼkuwapaka magazi mʼmunsi pakhutu lawo lakumanja, pachala chawo chamanthu kudzanja lamanja ndi pachala chawo chachikulu cha mwendo wakumanja. Koma magazi otsalawo, Mose anawawaza mbali zonse za guwa lansembe.+
25 Atatero anatenga mafuta a nkhosayo, mchira wa mafuta, mafuta onse okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wakumanja.+ 26 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala. Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wakumanja. 27 Atatero anaika zonsezi mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake nʼkuyamba kuziyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova. 28 Kenako Mose anazitenga mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza. Zinthu zimenezi zinali nsembe yowaikira kuti akhale ansembe, yakafungo kosangalatsa.* Inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
29 Kenako Mose anatenga chidale nʼkuchiyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova.+ Chidale chimenechi anachitenga pa nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe ndipo chinakhala gawo la Mose, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+
30 Ndipo Mose anatenga ena mwa mafuta odzozera+ ndi magazi amene anali paguwa lansembe aja nʼkuwaza Aroni ndi zovala zake komanso ana ake ndi zovala zawo. Choncho anapatula Aroni ndi zovala zake komanso ana ake+ ndi zovala zawo.+
31 Ndiyeno Mose anauza Aroni ndi ana ake kuti: “Wiritsani+ nyamayo pakhomo la chihema chokumanako, ndipo muidyerenso pomwepo pamodzi ndi mkate umene uli mʼdengu logwiritsidwa ntchito poika anthu kuti akhale ansembe, mogwirizana ndi zimene anandilamula kuti, ‘Aroni ndi ana ake adye zimenezi.’+ 32 Ndipo nyama ndi mkate zotsala muziwotche pamoto.+ 33 Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kwa masiku 7, mpaka masiku okuikani kuti mukhale ansembe atatha, chifukwa padzatenga masiku 7 kuti muikidwe kukhala ansembe.+ 34 Yehova walamula kuti tichite zomwe tachita lerozi kuti machimo anu aphimbidwe.+ 35 Mukhale pakhomo la chihema chokumanako masana ndi usiku kwa masiku 7.+ Ndipo muyenera kuchita zonse zimene Yehova walamula,+ kuti musafe. Chifukwa ndi zimene ndalamulidwa.”
36 Choncho Aroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.
9 Pa tsiku la 8,+ Mose anaitana Aroni, ana ake ndi akulu a Isiraeli. 2 Iye anauza Aroni kuti: “Tenga ngʼombe yaingʼono kuti ikhale nsembe yamachimo+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Nyama zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke kwa Yehova. 3 Koma Aisiraeli uwauze kuti, ‘Tengani mbuzi yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo. Mutengenso mwana wa ngʼombe ndi nkhosa yaingʼono yamphongo, zonsezi zikhale za chaka chimodzi, zopanda chilema, kuti zikhale nsembe yopsereza. 4 Mutengenso ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo kuti muzipereke kwa Yehova monga nsembe zamgwirizano.+ Komanso mubwere ndi nsembe yambewu+ yothira mafuta chifukwa lero Yehova aonekera kwa inu.’”+
5 Choncho anthuwo anatenga zimene Mose analamula nʼkupita nazo kuchihema chokumanako. Kenako gulu lonse linayandikira nʼkuima pamaso pa Yehova. 6 Ndiyeno Mose anati: “Izi ndi zimene Yehova wakulamulani kuti muchite, kuti ulemerero wa Yehova uonekere kwa inu.”+ 7 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo ako+ ndi a nyumba yako.* Ukatero uwaperekere nsembe anthuwa+ nʼkuwaphimbira machimo awo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”
8 Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe nʼkupha ngʼombe yaingʼono kuti ikhale nsembe yake+ yamachimo. 9 Ndiyeno ana ake anamubweretsera magazi+ a ngʼombeyo ndipo iye anaviika chala chake mʼmagaziwo nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe. Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo.+ 10 Ndipo mafuta, impso ndi mafuta apachiwindi zimene anazitenga panyama ya nsembe yamachimo anaziwotcha paguwa lansembe, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+ 11 Koma nyama ndi chikopa chake anaziwotcha kunja kwa msasa.+
12 Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza ndipo ana ake anamupatsa magazi a nyamayo. Atatero iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 13 Kenako anamʼpatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu ndipo anaziwotcha paguwa lansembe. 14 Atatero anatsuka matumbo komanso ziboda, nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza.
15 Ndiyeno anaperekera nsembe anthu. Anatenga mbuzi yoperekera anthu nsembe yamachimo ndipo anaipha, nʼkuipereka monga nsembe yamachimo, mmene anachitira ndi nyama yoyamba ija. 16 Atatero anapereka nsembe yopsereza motsatira ndondomeko yake.+
17 Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake nʼkuiwotcha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mʼmawa.+
18 Ndiyeno Aroni anapha ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yamgwirizano yoperekera anthuwo. Kenako ana ake anamupatsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 19 Koma mafuta a ngʼombeyo,+ mchira wa mafuta wa nkhosa, mafuta okuta ziwalo za mʼmimba, impso ndi mafuta apachiwindi,+ 20 ana a Aroni anaika mafuta amenewo pamwamba pa zidale za nyamazo. Kenako anawotcha mafutawo paguwa lansembe.+ 21 Koma Aroni anayendetsa uku ndi uku zidalezo ndi mwendo wakumbuyo wakumanja pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Mose analamula.+
22 Kenako Aroni anakweza manja ake nʼkuloza anthuwo ndipo anawadalitsa.+ Atatero anatsika kuguwa lansembe atamaliza kupereka nsembe yamachimo, nsembe yopsereza ndi nsembe zamgwirizano. 23 Pamapeto pake Mose ndi Aroni analowa mʼchihema chokumanako, kenako anatulukamo nʼkudalitsa anthuwo.+
Atatero ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse,+ 24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ nʼkunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi anayamba kufuula mokondwera ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
10 Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ omwe ndi ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira, nʼkuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Atatero anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule. 2 Choncho moto unatsika kuchokera kwa Yehova nʼkuwawotcha,+ moti anafa pamaso pa Yehova.+ 3 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Anthu amene ali pafupi ndi ine+ azikumbukira kuti ndine woyera, ndipo anthu onse adzandipatsa ulemerero.’” Koma Aroni anangokhala chete.
4 Zitatero, Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli,+ bambo aangʼono a Aroni, nʼkuwauza kuti: “Bwerani muchotse abale anu patsogolo pa malo oyera, mupite nawo kunja kwa msasa.” 5 Iwo anabweradi nʼkuwanyamula osawavula mikanjo yawo ndipo anapita nawo kunja kwa msasa, mogwirizana ndi zimene Mose ananena.
6 Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara kuti: “Musasiye tsitsi lanu osalisamala kapena kungʼamba zovala zanu+ kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire gulu lonseli. Abale anu omwe ndi nyumba yonse ya Isiraeli ndi amene alire anthu amene Yehova wawapha ndi moto. 7 Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kuopera kuti mungafe, chifukwa mwadzozedwa ndi mafuta odzozera a Yehova.”+ Choncho iwo anachita mogwirizana ndi zimene Mose ananena.
8 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: 9 “Mukamabwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa,+ kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 10 Mukamachita zimenezi mudzatha kusiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa ndiponso pakati pa chodetsedwa ndi choyera.+ 11 Komanso mudzatha kuphunzitsa Aisiraeli malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzera mwa Mose.”+
12 Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala kuti: “Tengani nsembe yambewu imene yatsala pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda zofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe,+ chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+ 13 Mudye nsembeyo mʼmalo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi nʼzimene ndalamulidwa. 14 Mudyenso chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndi mwendo wa gawo lopatulika.+ Muzidyere pamalo amene ayeretsedwa, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muzichita zimenezi chifukwa zinthu zimenezi zaperekedwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zamgwirizano za Aisiraeli. 15 Iwo azibweretsa mwendo wa gawo lopatulika ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, pamodzi ndi mafuta a nsembe zowotcha pamoto, kuti woperekayo aziyendetse uku ndi uku pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala gawo lanu ndi gawo la ana anu mpaka kalekale,+ mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”
16 Ndiyeno Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yamachimo,+ koma anaona kuti yonse inali itawotchedwa pamoto. Choncho iye anakwiyira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, ndipo anati: 17 “Nʼchifukwa chiyani simunadye nsembe yamachimo mʼmalo oyera?+ Nsembe imeneyi ndi yopatulika koposa, ndipo Mulungu wakupatsani kuti munyamule zolakwa za gulu lonse, ndi kuphimba machimo a gulu lonseli pamaso pa Yehova. 18 Taonani, simunabweretse magazi ake mkati, mʼmalo oyera.+ Munafunika kudya nsembeyo mʼmalo oyera, mogwirizana ndi zimene Mulungu anandilamula.” 19 Aroni anayankha Mose kuti: “Lero apereka nsembe yawo yamachimo ndi nsembe yawo yopsereza kwa Yehova,+ komabe zinthu izi zandigwera. Ndiye ndikanati ndadya nsembe yamachimo lero, kodi Yehova zikanamusangalatsa?” 20 Mose atamva zimenezi, anakhutira.
11 Kenako Yehova analankhula ndi Mose komanso Aroni kuti: 2 “Uzani Aisiraeli kuti, ‘Zamoyo zapadziko lapansi* zimene mungadye+ ndi izi: 3 Mungadye nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawanika zokhala ndi mpata pakati, yomwenso imabzikula.
4 Koma musamadye nyama zotsatirazi zimene zimabzikula kapena zili ndi ziboda zogawanika: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+ 5 Ndiponso mbira,+ chifukwa imabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Ndi yodetsedwa kwa inu. 6 Chimodzimodzinso kalulu, chifukwa amabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Ndi wodetsedwa kwa inu. 7 Komanso nkhumba,+ chifukwa ziboda zake nʼzogawanika ndipo zili ndi mpata pakati, koma siibzikula. Ndi yodetsedwa kwa inu. 8 Musamadye nyama iliyonse ya zimenezi, ndipo nyamazi zikafa musamazikhudze. Ndi zodetsedwa kwa inu.+
9 Zimene mungadye pa zonse zamʼmadzi ndi izi: Chilichonse chamʼmadzi chimene chili ndi zipsepse ndi mamba, kaya chimapezeka mʼnyanja kapena mʼmitsinje mungadye.+ 10 Koma chilichonse chopezeka mʼnyanja ndi mʼmitsinje chimene chilibe zipsepse ndi mamba, pa zamoyo zopezeka zambiri ndi pa zamoyo zina zonse zamʼmadzi, ndi zonyansa kwa inu. 11 Zinthu zimenezi zikhale zonyansa kwa inu. Musamadye nyama yake iliyonse,+ ndipo zikafa zizikhalabe zonyansa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse chamʼmadzi chimene chilibe zipsepse ndi mamba, ndi chonyansa kwa inu.
13 Izi ndi zamoyo zouluka zimene muyenera kuziona kuti ndi zonyansa. Sizikuyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: chiwombankhanga,+ nkhwazi, muimba wakuda,+ 14 mphamba wofiira, mtundu uliwonse wa mphamba wakuda, 15 mtundu uliwonse wa khwangwala, 16 nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa, mtundu uliwonse wa kabawi, 17 nkhwezule, chiswankhono, mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, muimba, 19 dokowe, mtundu uliwonse wa chimeza, sadzu ndi mleme. 20 Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu.
21 Pa tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso timayenda ndi miyendo yonse 4, mungathe kudya tizilombo tokhato timene tili ndi miyendo iwiri italiitali yolumphira. 22 Tizilombo timene mungadye ndi iti: mitundu yosiyanasiyana ya dzombe loyenda mitunda italiitali, mitundu ina ya dzombe lodyedwa,+ nkhululu ndi ziwala. 23 Koma tizilombo tina tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu. 24 Zamoyo zimenezi nʼzimene mungadzidetse nazo. Aliyense wokhudza zamoyo zimenezi zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 25 Aliyense wonyamula chilichonse mwa zamoyo zimenezi chitafa, azichapa zovala zake,+ ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
26 Nyama iliyonse imene ili ndi chiboda chogawanika koma chopanda mpata pakati, imenenso siibzikula, ndi yodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza nyama imeneyi adzakhala wodetsedwa.+ 27 Chamoyo chilichonse chokhala ndi mapazi a zikhadabo pa zamoyo zonse zimene zimayenda ndi miyendo yonse 4, nʼchodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza chamoyo chimenechi chitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28 Munthu wonyamula iliyonse ya nyama zimenezi itafa, azichapa zovala zake+ ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Nyama zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.
29 Izi ndi zamoyo zapadziko lapansi zomwe ndi zodetsedwa kwa inu: Mfuko, mbewa+ ndi mtundu uliwonse wa buluzi. 30 Ndiponso nalimata, buluzi wamkulu, dududu, buluzi wamumchenga ndi bilimankhwe. 31 Zamoyo zimenezi, zomwe zimapezeka zambiri, ndi zodetsedwa kwa inu.+ Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+
32 Ndiye chilichonse cha zamoyo zimenezi chikafa nʼkugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chidzakhala chodetsedwa, kaya ndi chiwiya chamtengo, chovala, chikopa kapena chiguduli. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziviikidwa mʼmadzi, ndipo chizikhala chodetsedwa mpaka madzulo, kenako chidzakhala choyera. 33 Ngati chamoyocho chagwera mʼchiwiya chadothi, muzichiswa, ndipo chilichonse chimene chinali mmenemo chidzakhala chodetsedwa.+ 34 Madzi a mʼchiwiya chimenecho akagwera pachakudya chilichonse, chakudyacho chizikhala chodetsedwa. Ndipo chakumwa chilichonse chimene chili mʼchiwiya chimenecho, chidzakhala chodetsedwa. 35 Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikafa nʼkugwera pachinthu chilichonse, kaya ndi uvuni kapena mbaula, chinthucho chidzakhala chodetsedwa ndipo muzichiswa. Zinthu zimenezi zadetsedwa ndipo zidzapitiriza kukhala zodetsedwa kwa inu. 36 Kasupe ndiponso thanki yosungiramo madzi ndi zokhazo zimene zidzakhalabe zoyera, koma aliyense wokhudza chinthu chakufacho adzakhala wodetsedwa. 37 Ngati chinthu chakufacho chagwera pambewu iliyonse imene mukufuna kudzala, mbewuyo izikhalabe yoyera. 38 Koma mbewuyo ikathiridwa madzi ndipo chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo nʼkugwerapo, mbewuyo izikhala yodetsedwa kwa inu.
39 Nyama iliyonse imene mwaloledwa kudya ikapezeka itafa, aliyense wokhudza nyama yakufayo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 40 Aliyense amene angadye nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Aliyense amene anganyamule nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 41 Zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi ndi zonyansa.+ Simukuyenera kudya zimenezi. 42 Musamadye chamoyo chilichonse chokwawa, chamoyo chilichonse chimene chimayenda ndi miyendo yonse 4 kapena zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi, zokhala ndi miyendo yambiri, chifukwa zimenezi ndi zonyansa.+ 43 Musamadziipitse ndi zamoyo zilizonse zimene zimapezeka zambirizi ndipo musamadzidetse nazo nʼkukhala odetsedwa.+ 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Mudzipatule ndi kukhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+ Choncho musamadzidetse ndi chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu.+ Muzikhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+
46 Limeneli ndi lamulo lokhudza nyama, zamoyo zouluka, zamoyo zonse zamʼmadzi ndi zamoyo zonse zapamtunda, 47 kuti muzisiyanitsa chodetsedwa ndi choyera komanso zamoyo zimene muyenera kudya ndi zimene simukuyenera kudya.’”+
12 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba.+ 3 Pa tsiku la 8, mwanayo azidulidwa.+ 4 Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 33. Asamakhudze chilichonse chopatulika komanso asamalowe mʼmalo oyera mpaka atakwanitsa masiku a kuyeretsedwa kwake.
5 Akabereka mwana wamkazi, azikhala wodetsedwa kwa masiku 14 ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba. Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 66. 6 Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo. 7 Wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kumʼphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera pa kukha magazi kwake. Limeneli ndi lamulo lokhudza mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi. 8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi izikhala ya nsembe yopsereza, inayo izikhala ya nsembe yamachimo. Akatero wansembe adzamuphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera.’”
13 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni kuti: 2 “Munthu akatuluka chotupa, kapena nkhanambo,* kapena chikanga, moti ingathe kukhala nthenda ya khate*+ pakhungu lake, azibwera naye kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake omwenso ndi ansembe.+ 3 Wansembeyo aziona nthenda imene yatuluka pakhunguyo. Ngati cheya chapamalopo chasanduka choyera ndipo pakuoneka kuti nthendayo yalowa mpaka mkati mwa khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe aziona nthendayo nʼkugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. 4 Koma ngati chikangacho chikuoneka choyera ndipo sichinalowe mkati mwa khungu, komanso cheya sichinasanduke choyera, wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku 7.+ 5 Ndiyeno wansembe azionanso munthuyo pa tsiku la 7, ndipo ngati nthendayo ikuoneka kuti yatha, moti sinafalikire pakhungu, wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku enanso 7.
6 Wansembe azionanso munthuyo kachiwiri pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yatheratu ndipo sinafalikire pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Inangokhala nkhanambo basi. Kenako munthuyo azichapa zovala zake nʼkukhala woyera. 7 Koma ngati nkhanambo yafalikira pakhungu la munthu pambuyo poti anaonekera kwa wansembe ndipo anagamula kuti ndi woyera, munthuyo azikaonekeranso kachiwiri kwa wansembe. 8 Wansembe azionanso munthuyo ndipo ngati nkhanambo yake yafalikira pakhungu, wansembeyo azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate.+
9 Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, azimubweretsa kwa wansembe. 10 Wansembe azimuona+ ndipo ngati pakhungupo pali chotupa moti khungu ndi cheya zayera, ndipo pachotupapo pali chilonda,+ 11 limenelo ndi khate lokhalitsa pakhungu lake, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamuike kwayekha*+ chifukwa ndi wodetsedwa. 12 Koma ngati khate layamba pakhungu lake, moti wansembe akuchita kuoneratu kuti lafalikira pathupi lonse la munthuyo, kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13 ndipo wansembe wamuona, nʼkutsimikizira kuti khatelo lafalikiradi thupi lonse, pamenepo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.* Khungu lake lonse latuwa, choncho ndi woyera. 14 Koma akadzatuluka zilonda, ndiye kuti adzakhala wodetsedwa. 15 Wansembe akaona zilondazo, azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa+ chifukwa cha zilondazo. Limenelo ndi khate.+ 16 Koma ngati zilondazo zasandukanso zoyera, munthuyo azibwera kwa wansembe. 17 Ndiyeno wansembe azimuona+ ndipo ngati khungu lake latuwa, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.
18 Ngati munthu anali ndi chithupsa pakhungu lake, ndiye kenako chapola, 19 koma pamene panali chithupsapo patuluka chotupa choyera kapena chikanga chotuwa mofiirira, munthuyo azikaonekera kwa wansembe. 20 Wansembe aziona chotupacho.+ Ngati chikuoneka kuti chayambira mkati mwa khungu ndipo cheya chake chasanduka choyera, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo yatuluka pachithupsacho. 21 Koma wansembe akachiona nʼkupeza kuti palibe cheya choyera ndipo sichinayambire mkati mwa khungu komanso chikuoneka kuti chikutha, wansembe azimuika kwayekha kwa masiku 7.+ 22 Ngati chikangacho chafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda. 23 Koma ngati chikangacho chili pamalo amodzi ndipo sichinafalikire, kumeneko ndi kutukusira kwa chithupsa. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+
24 Kapena ngati pakhungu pali bala lamoto, ndipo mnofu wapabalapo wayamba kuoneka wotuwa mofiirira kapena woyera, 25 wansembe aziona balalo. Ngati cheya cha pamalopo chasanduka choyera ndipo balalo likuoneka lozama kuposa khungu, limenelo ndi khate. Latuluka pabala, ndipo wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 26 Koma ngati wansembe waona balalo, nʼkupeza kuti palibe cheya choyera ndipo balalo si lozama kuposa khungu komanso likutha, wansembe azimuika kwayekha kwa masiku 7.+ 27 Wansembe aziona munthuyo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. 28 Koma ngati chikangacho chili pamalo amodzi ndipo sichinafalikire pakhungu komanso chikutha, kumeneko ndi kutupa kwa bala. Wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera chifukwa kumeneko ndi kutukusira kwa bala.
29 Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi nthenda ina yake pamutu kapena pachibwano, 30 wansembe aziona nthendayo.+ Ngati pamalopo pakuoneka kuti nthendayo yalowa mkati mwa khungu, komanso tsitsi lachita chikasu ndipo lili patalipatali, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya pamutu ndi ndevu. Ndi khate lakumutu kapena kuchibwano. 31 Koma ngati wansembe waona kuti nthendayo sinalowe mkati mwa khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda, wansembe aziika munthuyo kwayekha kwa masiku 7.+ 32 Wansembe azionanso nthendayo pa tsiku la 7. Ngati nthendayo sinafalikire, komanso pamalopo sipanamere tsitsi lachikasu ndipo pakuoneka kuti sinalowe mkati mwa khungu, 33 munthuyo azimetedwa tsitsi lake, koma asamamʼmete pamene pali nthendapo. Kenako wansembe azimuika munthuyo kwayekha kwa masiku 7.
34 Pa tsiku la 7 wansembe azionanso nthendayo. Ngati nthenda yapamutu ndi yapandevu sinafalikire pakhungu, ndipo zikuoneka kuti nthendayo sinalowe mkati mwa khungu, wansembe azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Akatero munthuyo azichapa zovala zake nʼkukhala woyera. 35 Koma ngati nthendayo yafalikiradi pakhungu pambuyo poti munthuyo wagamulidwa kuti ndi woyera, 36 wansembe azionanso munthuyo. Ngati nthendayo yafalikira pakhungu, wansembe sakuyenera kufufuzanso tsitsi lachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37 Koma ngati nthendayo ikuoneka kuti sinafalikire ndipo pamalopo pamera tsitsi lakuda, ndiye kuti nthendayo yatha. Munthuyo ndi woyera ndipo wansembe azigamula kuti ndi woyera.+
38 Mwamuna kapena mkazi akagwidwa ndi zikanga zotuwa pakhungu lake, 39 wansembe aziziona.+ Ngati zikangazo zayamba kutha, imeneyo ndi nthenda yosaopsa imene yatuluka pakhungu lake. Munthuyo ndi woyera.
40 Mwamuna akayamba kutha tsitsi kumutu nʼkuchita dazi, ndi woyera. 41 Ngati tsitsi latha patsogolo pa mutu wake nʼkuchita dazi, ndi woyera. 42 Koma ngati padazi lake kapena pamphumi pake patuluka chilonda chotuwa mofiirira, limenelo ndi khate, latuluka pamutu pake kapena pamphumi pake. 43 Wansembe aziona munthuyo, ndipo ngati kutupa kwa chilondacho kukuoneka kotuwa mofiirira padazipo kapena pamphumi pake, ndipo zikuoneka ngati pakhungu lakelo pali khate, 44 ameneyo ali ndi khate. Munthuyo ndi wodetsedwa, ndipo wansembe azigamula kuti ndi wodetsedwa chifukwa cha nthenda imene ili pamutu pake. 45 Munthu amene ali ndi khateyo, zovala zake zizingʼambidwa ndipo asamakonze tsitsi lake. Koma aziphimba ndevu zake zapamlomo nʼkumafuula kuti, ‘Wodetsedwa, wodetsedwa!’ 46 Azikhala wodetsedwa pa nthawi yonse imene akudwala nthendayo. Chifukwa chakuti ndi wodetsedwa, azikhala kwayekha. Azikhala kunja kwa msasa.+
47 Ngati nthenda ya khate yadetsa chovala, kaya chovalacho ndi chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, 48 kaya ili mulitali kapena mulifupi* mwa chovala chansalu kapena chaubweya wa nkhosa, kapenanso pachikopa kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, 49 ndipo nthendayo ikuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pachovala kapena pachikopa, mulitali kapena mulifupi mwa nsalu, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nthenda ya khate ndipo chinthucho muyenera kukachionetsa kwa wansembe. 50 Wansembe aziona nthendayo, ndipo azisunga chinthucho kwachokha kwa masiku 7.+ 51 Akaona nthendayo pa tsiku la 7 nʼkupeza kuti yafalikira pachovala, mulitali kapena mulifupi, kapena pachikopa (kaya chikopacho amachigwiritsa ntchito yotani), nthendayo ndi khate loopsa ndipo chinthucho nʼchodetsedwa.+ 52 Aziwotcha chovalacho, nsalu ya ubweya wa nkhosa kapena nsalu ina iliyonse, kapena zilizonse zopangidwa ndi chikopa, zimene zagwidwa ndi nthenda ya khateyo, chifukwa khate limenelo ndi loopsa. Ziziwotchedwa pamoto.
53 Koma wansembeyo akaona, nʼkupeza kuti nthendayo sinafalikire pachovalacho, mulitali kapena mulifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, 54 wansembe azilamula kuti achape chinthu chogwidwa ndi nthendacho ndipo azichisunga kwachokha kwa masiku enanso 7. 55 Wansembe aziona chinthu chimene chili ndi nthendacho, chinthucho chitachapidwa. Ngakhale kuti nthendayo ikuonekabe chimodzimodzi ndipo sinafalikire, chinthucho ndi chodetsedwa. Muzichiwotcha pamoto chifukwa chadyedwa ndi nthendayo kuyambira mkati kapena kuyambira kunja kwake.
56 Koma ngati wansembe waona chinthucho, nʼkupeza kuti nthenda ija yatha chinthucho chitachapidwa, azingʼamba mbali yogwidwa ndi nthendayo pachovalacho kapena pachikopacho. 57 Koma ngati nthendayo ikuonekabe mbali ina ya chovalacho, mulitali kapena mulifupi, kapena pa chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nthendayo ikufalikira. Chilichonse chimene chagwidwa ndi nthendayi muzichiwotcha pamoto.+ 58 Koma ngati nthendayo yatha mutachapa chovalacho kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, muzichichapanso kachiwiri, ndipo chidzakhala choyera.
59 Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda ya khate yopezeka pachovala chaubweya wa nkhosa kapena chansalu, mulitali kapena mulifupi, kapena pachinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti wansembe adziwe chinthu choyenera kugamula kuti nʼchoyera kapena nʼchodetsedwa.”
14 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Ili likhale lamulo lokhudza wakhate pa tsiku limene adzamubweretse kwa wansembe+ pa nthawi yoti ayeretsedwe. 3 Wansembe azipita kunja kwa msasa kukamuona. Ngati munthuyo wachira khate lake, 4 wansembe azimulamula kuti abweretse mbalame zamoyo ziwiri zosadetsedwa, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope* kuti adzazigwiritse ntchito pomuyeretsa.+ 5 Ndipo wansembe azilamula kuti mbalame imodzi aiphere pamwamba pa madzi otunga kumtsinje, amene ali mʼchiwiya chadothi. 6 Koma azitenga mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope, nʼkuviika zinthu zonsezi mʼmagazi a mbalame imene aiphera pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija. 7 Kenako wansembe azidontheza magaziwo maulendo 7 pamunthu amene akudziyeretsa ku khateyo, ndipo azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Akatero aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo.+
8 Munthu amene akudziyeretsayo azichapa zovala zake ndi kumeta tsitsi lake lonse, kenako azisamba ndipo azikhala woyera. Akatero angathe kulowa mumsasa, koma azikhala kunja kwa tenti yake kwa masiku 7. 9 Pa tsiku la 7 azimeta tsitsi lake lonse lakumutu, ndevu zake zonse ndi nsidze zonse. Akamaliza kumeta tsitsi lake lonse azichapa zovala zake nʼkusamba mʼmadzi ndipo adzakhala woyera.
10 Pa tsiku la 8, iye adzatenge nkhosa zazingʼono zamphongo ziwiri zopanda chilema komanso nkhosa yaingʼono yaikazi+ imodzi yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi. Adzatengenso ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake ya mbewu+ yothira mafuta ndi muyezo umodzi* wa mafuta.+ 11 Ndipo wansembe amene wagamula kuti munthuyo ndi woyera, azionetsa amene akudziyeretsayo, limodzi ndi zinthu zakezo kwa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 12 Wansembeyo azidzatenga nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi nʼkuipereka monga nsembe yakupalamula+ pamodzi ndi muyezo umodzi wa mafuta uja. Zimenezi aziziyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ 13 Kenako azipha nkhosa yaingʼono yamphongoyo pamalo amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza,+ pamalo oyera. Azichita zimenezi chifukwa nsembe yakupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe yakupalamula ndi yopatulika koposa.+
14 Ndiyeno wansembe azidzatenga ena mwa magazi a nsembe yakupalamula, nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja. 15 Akatero, wansembeyo azitenga ena mwa mafuta pamuyezo umodzi+ uja nʼkuwathira pachikhatho cha dzanja lake lamanzere. 16 Kenako wansembe aziviika chala chake chakudzanja lamanja mʼmafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzere, ndipo azidontheza pansi ena mwa mafutawo ndi chala chakecho maulendo 7, pamaso pa Yehova. 17 Koma mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja pamene anamupaka magazi a nsembe yakupalamula. 18 Mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, ndipo wansembe adzamuphimbira machimo ake pamaso pa Yehova.+
19 Wansembe adzapereke nsembe yamachimo+ nʼkuphimba machimo a munthu amene akudziyeretsayo. Kenako wansembe adzaphe nyama ya nsembe yopsereza. 20 Ndiyeno wansembe adzapereke nsembe yopsereza ndi nsembe yambewu+ paguwa lansembe. Akatero, wansembe adzamuphimbira machimo,+ ndipo munthuyo adzakhala woyera.+
21 Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu. 22 Komanso azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, mogwirizana ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+ 23 Pa tsiku la 8+ azibweretsa zinthuzi kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova,+ kuti wansembeyo agamule kuti munthuyo ndi woyera.
24 Kenako wansembe azitenga nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yakupalamula+ ndi muyezo umodzi wa mafuta uja, ndipo wansembeyo aziyendetsa zinthu zimenezi uku ndi uku, monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ 25 Ndiyeno wansembe azipha nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yakupalamula. Akatero azitenga ena mwa magazi a nsembe yakupalamulayo nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja.+ 26 Wansembeyo adzathire ena mwa mafutawo pachikhatho cha dzanja lake lamanzere.+ 27 Akatero adzadontheze ndi chala chake cha dzanja lamanja ena mwa mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzerewo maulendo 7 pamaso pa Yehova. 28 Kenako wansembe adzapake ena mwa mafuta amene ali pachikhatho chake, mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja pamene anamupaka magazi a nsembe yakupalamula ija. 29 Ndiyeno mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, kuti amuphimbire machimo ake pamaso pa Yehova.
30 Kenako wansembe azipereka mmodzi mwa ana a njiwa kapena mmodzi mwa ana a nkhunda, mogwirizana ndi zimene munthuyo angakwanitse.+ 31 Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza,+ azipereka imene angakwanitse pamodzi ndi nsembe yambewu. Ndipo wansembe aziphimba machimo a munthu amene akudziyeretsayo pamaso pa Yehova.+
32 Limeneli ndi lamulo lokhudza munthu amene ali ndi nthenda ya khate, amene sangakwanitse kupeza zinthu zimene zimafunika pa tsiku la kuyeretsedwa kwake.”
33 Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 34 “Mukakafika mʼdziko la Kanani,+ limene ine ndikukupatsani kuti likhale lanu,+ ndipo ndikadzalola nthenda ya khate kuti ikhale mʼnyumba ina mʼdziko lanulo,+ 35 mwiniwake wa nyumbayo azibwera kwa wansembe nʼkumuuza kuti, ‘Ndaona chinachake chooneka ngati nthenda ya khate mʼnyumba mwanga.’ 36 Wansembe adzalamula kuti atulutse katundu mʼnyumbamo iye asanafike kudzaona nthendayo. Adzachite zimenezi kuti wansembe asadzagamule kuti chilichonse mʼnyumbamo nʼchodetsedwa. Kenako wansembe adzabwere kudzaona nyumbayo. 37 Akaona nthendayo nʼkupeza kuti ili mʼmakoma a nyumba, ndipo ikuoneka ngati mawanga obiriwira mopitira ku chikasu kapena ofiirira, komanso mawangawo akuoneka kuti alowa mkati mwa khoma, 38 wansembe azituluka mʼnyumbamo nʼkukaima pakhomo, ndipo azitseka nyumbayo masiku 7.+
39 Kenako pa tsiku la 7, wansembe azibweranso kudzaona nyumbayo. Ngati nthendayo yafalikira mʼmakoma ake, 40 wansembe azilamula kuti achotse miyala imene ili ndi nthendayo, nʼkukaiponya kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 41 Ndiyeno wansembe alamule kuti apale mkati mwa nyumba yonseyo, nʼkukataya zimene apalazo kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 42 Akatero azitenga miyala ina nʼkumanga pamene panali miyala yakaleyo. Kenako aziwalamula kuti apange pulasitala nyumbayo ndi dothi lina.
43 Koma ngati nthendayo yabwerera nʼkufalikiranso mʼnyumbamo, atachotsa miyala ija, kupala nyumbayo nʼkuipanganso pulasitala, 44 wansembe azibweranso kudzaiona. Ngati nthendayo yafalikira mʼnyumbamo, limenelo ndi khate loopsa.+ Nyumbayo ndi yodetsedwa. 45 Kenako azilamula kuti nyumbayo aigwetse pamodzi ndi miyala yake, matabwa ake ndi dothi lake lonse lomangira, ndipo zonsezi azitengere kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa.+ 46 Koma aliyense wolowa mʼnyumbayo pa masiku amene wansembe walamula kuti munthu asalowemo,+ azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 47 Aliyense amene wagona mʼnyumbamo ndiponso aliyense amene wadyeramo chakudya azichapa zovala zake.
48 Koma ngati wansembe wabwera kudzaona nyumbayo ataipanganso pulasitala nʼkupeza kuti nthendayo sinafalikire mʼnyumbayo, wansembe azigamula kuti nyumbayo ndi yoyera chifukwa nthendayo yatha. 49 Ndiyeno kuti ayeretse nyumbayo, azitenga mbalame ziwiri, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope.+ 50 Wansembe azipha mbalame imodzi pamwamba pa madzi akumtsinje, amene ali mʼchiwiya chadothi. 51 Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope, ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika mʼmagazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo. 52 Ndiyeno aziyeretsa nyumbayo pogwiritsa ntchito magazi a mbalame ija, madzi otunga kumtsinje, mbalame yamoyo ija, nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope ndi ulusi wofiira kwambiri. 53 Kenako aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo, kunja kwa mzinda. Akatero aziyeretsa nyumbayo, ndipo idzakhala yoyera.
54 Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda iliyonse ya khate, nthenda yapamutu kapena pandevu,+ 55 khate lapachovala+ kapena lamʼnyumba,+ 56 zotupa, nkhanambo* ndi zikanga.+ 57 Lamulo limeneli laperekedwa kuti akhale malangizo othandiza kudziwa ngati chinthu chili chodetsedwa kapena choyera.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda ya khate.”+
15 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ngati mwamuna ali ndi nthenda ya kukha kumaliseche, nthenda yakeyo ikumupangitsa kukhala wodetsedwa.+ 3 Iye ndi wodetsedwa chifukwa cha zimene zikukhazo, kaya zinthuzo zikupitirizabe kutuluka kapena maliseche ake atsekeka ndi zimene zikukhazo, azikhalabe wodetsedwa.
4 Bedi lililonse limene munthu amene akukhayo angagonepo lizikhala lodetsedwa, ndipo chilichonse chimene angakhalepo chizikhala chodetsedwa. 5 Munthu amene wakhudza bedi lakelo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 6 Aliyense wokhala pachinthu chimene munthu amene akukhayo anakhalapo, azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 7 Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akukhayo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 8 Ngati amene akukhayo walavulira munthu woyera, munthuyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 9 Chishalo chilichonse chimene munthu amene akukhayo anakhalapo chizikhala chodetsedwa. 10 Aliyense wokhudza chilichonse chimene munthuyo wakhalapo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ndipo munthu wonyamula zinthu zimenezi azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 11 Ngati munthu amene akukhayo+ wagwira munthu wina asanasambe mʼmanja, munthuyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 12 Chiwiya chadothi chimene munthu wanthenda yakukhayo wakhudza chiziswedwa, ndipo chikakhala chamtengo chizitsukidwa.+
13 Ndiyeno munthuyo akachira nthenda yake yakukhayo, pazipita masiku 7 kuti akhale woyera. Kenako azichapa zovala zake nʼkusamba madzi otunga kumtsinje, ndipo iye adzakhala woyera.+ 14 Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, nʼkuzipereka kwa wansembe. 15 Ndiyeno wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo.
16 Mwamuna akatulutsa umuna, azisamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 17 Azichapa chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse chimene pagwera umunawo, ndipo chizikhala chodetsedwa mpaka madzulo.
18 Mwamuna akagona ndi mkazi nʼkutulutsa umuna, onse awiri azisamba thupi lonse, ndipo azikhala odetsedwa mpaka madzulo.+
19 Ngati mkazi akukha magazi, azikhala masiku 7 ali wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba.+ Aliyense amene angamukhudze adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 20 Chilichonse chimene angagonepo pamene ali wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba chizikhala chodetsedwa, ndiponso chilichonse chimene wakhalapo chizikhala chodetsedwa.+ 21 Aliyense wokhudza bedi lake azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Aliyense wokhudza chilichonse chimene mkaziyo anakhalira azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23 Ndipo ngati mkaziyo anakhala pabedi kapena pachinthu china, aliyense wokhudza chinthu chimenecho azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 24 Mwamuna akagona ndi mkazi ameneyu, azikhala wodetsedwa chifukwa chakuti mkaziyo akusamba.+ Zikatero, mwamunayo azikhala wodetsedwa kwa masiku 7, ndipo bedi lililonse limene angagonepo lizikhala lodetsedwa.
25 Mkazi akakha magazi kwa masiku ambiri+ pamene si nthawi yake yosamba,+ kapena akapitiriza kukha magazi nthawi yake yosamba itatha, azikhala wodetsedwa masiku onse amene akukha magaziwo ngati mmene amakhalira pa nthawi yake yosamba. 26 Bedi lililonse limene angagonepo pa nthawi imene akukha magaziwo,+ lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi imene akusamba. Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa ngati mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi imene akusamba. 27 Aliyense amene angakhudze zinthuzo adzakhala wodetsedwa, ndipo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+
28 Akasiya kukha magaziwo, pazipita masiku 7, kenako azikhala woyera.+ 29 Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda,+ nʼkubwera nawo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+ 30 Wansembe azipereka mbalame imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Ndiyeno wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha kukhako.+
31 Muzionetsetsa kuti Aisiraeli akupewa chilichonse chodetsa, kuopera kuti angafe chifukwa chodetsa chihema changa chimene chili pakati pawo.+
32 Limeneli ndi lamulo lokhudza mwamuna amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche, ndi mwamuna amene ndi wodetsedwa chifukwa chakuti watulutsa umuna.+ 33 Lamulo limeneli ndi lokhudzanso mkazi wodetsedwa chifukwa chakuti akusamba,+ mwamuna kapena mkazi aliyense amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche,+ ndiponso mwamuna amene wagona ndi mkazi wodetsedwa.’”
16 Yehova analankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana awiri a Aroni, amene anafa chifukwa choonekera pamaso pa Yehova mosavomerezeka.+ 2 Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni mʼbale wako kuti asamalowe mʼmalo oyera+ kuseri kwa katani,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, pa nthawi iliyonse imene wafuna, kuopera kuti angafe+ chifukwa ine ndidzaonekera mumtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+
3 Polowa mʼmalo oyera, Aroni azitenga zotsatirazi: ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ 4 Azivala mkanjo wopatulika wansalu,+ kabudula wansalu+ wobisa* thupi lake, azimanga lamba wansalu wapamimba,+ ndipo azikulunga kumutu kwake ndi nduwira yansalu.+ Zimenezi ndi zovala zopatulika.+ Iye azivala zimenezi atasamba thupi lonse.+
5 Gulu la Aisiraeli lizimupatsa+ ana a mbuzi amphongo awiri kuti akhale nsembe yamachimo ndiponso nkhosa yamphongo imodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.
6 Akatero Aroni azibweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, ndipo aziphimba machimo ake+ ndi a banja lake.*
7 Kenako azitenga mbuzi ziwiri zija nʼkuziimika pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 8 Ndiyeno Aroni azichita maere pa mbuzi ziwirizo. Maere amodzi akhale a Yehova, ndipo ena akhale a mbuzi yotenga machimo a anthu.* 9 Aroni azibweretsa mbuzi imene maere asonyeza+ kuti ndi ya Yehova, ndipo izikhala nsembe yamachimo. 10 Koma mbuzi imene maere asonyeza kuti ndi yotenga machimo a anthu, aziibweretsa yamoyo nʼkuiimika pamaso pa Yehova kuti machimo a anthu aphimbidwe. Akatero aziitumiza mʼchipululu monga mbuzi yotenga machimo a anthu.+
11 Aroni azibweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, ndipo aziphimba machimo ake ndi a banja lake. Pambuyo pake azipha ngʼombe ya nsembe yake yamachimoyo.+
12 Kenako iye azitenga chofukizira+ chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri+ zokwana manja awiri odzaza nʼkulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa katani.+ 13 Akatero aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova,+ ndipo utsi wa zofukizazo uziphimba chivundikiro cha Likasa+ chimene chili pamwamba pa Umboni+ kuti asafe.
14 Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ngʼombe yamphongoyo+ nʼkuwadontheza ndi chala chake patsogolo pa chivundikiro, mbali ya kumʼmawa. Azidontheza magaziwo ndi chala chake maulendo 7 patsogolo pa chivundikirocho.+
15 Kenako azipha mbuzi ya nsembe yamachimo yoperekera anthuwo,+ nʼkulowa ndi magazi ake kuchipinda, kuseri kwa katani.+ Kumeneko magaziwo+ azichita nawo zimene anachita ndi magazi a ngʼombe yamphongo ija. Azidontheza magaziwo patsogolo pa chivundikiro.
16 Aziphimba machimo a malo oyera chifukwa cha zinthu zodetsa zimene Aisiraeli achita komanso chifukwa cha zolakwa ndi machimo awo.+ Azichita zimenezi ndi chihema chokumanako chimene chili pakati pa Aisiraeli, amene amachita zinthu zodetsa.
17 Mʼchihema chokumanako musamapezeke munthu wina aliyense kuyambira nthawi imene Aroni walowa mʼmalo oyera kukaphimba machimo mpaka kutulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake, a banja lake+ ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+
18 Akatero azituluka nʼkupita kuguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova kuti akaliphimbire machimo. Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ngʼombe yamphongo ndi a mbuzi nʼkuwapaka panyanga zonse za guwa lansembe. 19 Ena mwa magaziwo aziwadonthezera paguwalo ndi chala chake maulendo 7, kuti likhale lopatulika komanso kuti aliyeretse ku zinthu zodetsa za Aisiraeli.
20 Akamaliza kuphimbira machimo+ malo oyera, chihema chokumanako ndi guwa lansembe,+ azibweretsanso mbuzi yamoyo ija.+ 21 Ndipo Aroni aziika manja ake onse pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza zolakwa zonse za Aisiraeli ndiponso machimo awo onse. Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi+ ija nʼkuipereka kwa munthu amene amusankhiratu kuti akaisiye kuchipululu. 22 Mbuziyo izinyamula zolakwa zawo zonse+ pamutu pake ndipo aziitumiza kuchipululu.+
23 Kenako Aroni azilowa mʼchihema chokumanako nʼkuvula zovala zake zimene anavala polowa mʼmalo oyera, ndipo azizisiya momwemo. 24 Akatero azisamba thupi lonse+ mʼmalo oyera nʼkuvala zovala zake.+ Kenako azituluka nʼkukapereka nsembe yake yopsereza+ ndi nsembe yopsereza ya anthuwo+ ndipo aziphimba machimo ake ndi a anthuwo.+ 25 Ndiyeno aziwotcha mafuta a nsembe yamachimo paguwa lansembe.
26 Munthu amene anapititsa mbuzi yotenga machimo a anthu+ uja azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse. Akatero angathe kulowa mumsasa.
27 Ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo, zimene magazi ake analowa nawo mʼmalo oyera pokaphimba machimo, azipita nazo kunja kwa msasa ndipo aziwotcha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+ 28 Munthu amene wawotcha zimenezi azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, akatero angathe kulowa mumsasa.
29 Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo anu ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale. 30 Pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+ 31 Limeneli ndi sabata lanu lopuma pa ntchito zonse ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale.
32 Wansembe amene adzadzozedwe+ nʼkuikidwa* kuti atumikire monga wansembe,+ kulowa mʼmalo mwa bambo ake,+ aziphimba machimo ndipo azivala zovala za nsalu,+ zomwe ndi zovala zopatulika.+ 33 Iye aziphimba machimo a malo opatulika koposa,+ chihema chokumanako+ ndi guwa lansembe.+ Aziphimbanso machimo a ansembe ndi a mpingo wonse wa anthu.+ 34 Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale,+ kuti machimo onse a Aisiraeli aziphimbidwa kamodzi pa chaka.”+
Choncho iye anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aroni ndi ana ake komanso Aisiraeli onse kuti, ‘Izi ndi zimene Yehova walamula:
3 “Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli akapha ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi mumsasa, kapena kunja kwa msasa, 4 mʼmalo mobwera nayo pakhomo la chihema chokumanako, kuti aipereke monga nsembe kwa Yehova patsogolo pa chihema cha Yehova, ameneyo adzakhala ndi mlandu wa magazi. Munthu ameneyo wakhetsa magazi, ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 5 Lamulo limeneli laperekedwa kuti nsembe zimene Aisiraeli akuzipereka kunja, azibwera nazo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako kuti azipereke kwa Yehova. Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe zamgwirizano kwa Yehova.+ 6 Wansembe aziwaza magazi a nyamazo paguwa lansembe la Yehova limene lili pakhomo la chihema chokumanako, ndipo aziwotcha mafuta ake kuti likhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 7 Choncho asamaperekenso nsembe zawo kwa ziwanda zooneka ngati mbuzi+ zimene akuzilambira.*+ Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale, mʼmibadwo yanu yonse.”’
8 Uwauze kuti, ‘Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, amene wapereka nsembe yopsereza kapena nsembe iliyonse, 9 koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako kuti aipereke kwa Yehova, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+
10 Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, akadya magazi alionse,+ ndidzadana naye ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 11 Chifukwa moyo wa nyama uli mʼmagazi+ ndipo ine ndawapereka paguwa lansembe+ kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho chifukwa magazi ndi amene amaphimba machimo+ chifukwa cha moyo umene uli mʼmagaziwo. 12 Nʼchifukwa chake ndauza Aisiraeli kuti: “Aliyense wa inu asamadye magazi ndipo mlendo wokhala pakati panu+ asamadye magazi.”+
13 Ngati munthu wa Chiisiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu wapita kokasaka, ndipo wagwira nyama kapena mbalame imene munaloledwa kuti muzidya, azithira magazi ake pansi+ nʼkuwakwirira ndi dothi. 14 Moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake chifukwa mʼmagazimo ndi mmene muli moyo. Nʼchifukwa chake ndauza Aisiraeli kuti: “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.”+ 15 Ngati munthu aliyense wadya nyama imene waipeza yakufa kapena imene yaphedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Kenako azikhala woyera. 16 Koma ngati sanachape zovala zakezo komanso sanasambe thupi lonse, ameneyo ayenera kuyankha mlandu chifukwa cha kulakwa kwakeko.’”+
18 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 3 Musamachite zinthu zimene anthu a ku Iguputo kumene munkakhala amachita, komanso musamachite zinthu zimene anthu amʼdziko la Kanani limene ndikukupititsani amachita.+ Ndipo musamakatsatire malamulo awo. 4 Muzisunga zigamulo zanga komanso muzitsatira malamulo anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5 Muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova.
6 Mwamuna aliyense pakati panu asayandikire wachibale wake aliyense kuti agone naye.*+ Ine ndine Yehova. 7 Usagone ndi bambo ako komanso usagone ndi mayi ako. Amenewo ndi mayi ako ndipo usagone nawo.
8 Usagone ndi mkazi wa bambo ako,+ chifukwa kuchita zimenezo nʼkuchititsa manyazi bambo ako.*
9 Usagone ndi mchemwali wako, kaya ndi mwana wamkazi wa bambo ako kapena mwana wamkazi wa mayi ako. Kaya munabadwira mʼbanja limodzi kapena anabadwira mʼbanja lina.+
10 Usagone ndi mwana wamkazi wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wamkazi wa mwana wako wamkazi, chifukwa kumeneko nʼkudzichititsa manyazi.
11 Usagone ndi mwana wamkazi wa mkazi wa bambo ako, mwana wa bambo ako, chifukwa ameneyo ndi mchemwali wako.
12 Usagone ndi mchemwali wa bambo ako. Ameneyo ndi wachibale wa bambo ako.+
13 Usagone ndi mchemwali wa mayi ako, chifukwa ndi wachibale wa mayi ako.
14 Usachititse manyazi mchimwene wa bambo ako* mwa kugona ndi mkazi wake, chifukwa amenewo ndi mayi ako.+
15 Usagone ndi mpongozi wako wamkazi.+ Iye ndi mkazi wa mwana wako, choncho usagone naye.
16 Usagone ndi mkazi wa mchimwene wako,+ chifukwa kumeneko nʼkuchititsa manyazi* mchimwene wako.
17 Usagone ndi mkazi limodzi ndi mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo komanso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti ugone naye. Limeneli ndi khalidwe lonyansa* chifukwa amenewa ndi achibale a mkazi wako.
18 Ukakwatira mkazi usakwatirenso mchemwali wake kuti akhale mkazi wako wachiwiri,+ nʼkumagona naye mchemwali wakeyo ali moyo.
19 Usayandikire mkazi kuti ugone naye pa nthawi imene akusamba chifukwa ndi wodetsedwa.+
20 Usagone ndi mkazi wa mnzako nʼkukhala wodetsedwa.+
21 Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe* kwa Moleki.+ Usanyoze dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi.+ Ine ndine Yehova.
22 Usagone ndi mwamuna ngati mmene umagonera ndi mkazi.+ Zimenezi nʼzonyansa.
23 Mwamuna asamagone ndi nyama nʼkukhala wodetsedwa, ndipo mkazi asamadzipereke kwa nyama kuti agone nayo.+ Kuchita zimenezi nʼkosemphana ndi chibadwa.
24 Musamadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu yadzidetsa ndi makhalidwe onyansawa.+ 25 Nʼchifukwa chake dzikolo ndi lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha zolakwa zake moti dzikolo lidzalavula anthu ake kunja.+ 26 Koma inu muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga.+ Ndipo aliyense wa inu, kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, asamachite chilichonse cha zinthu zonyansa zimenezi.+ 27 Chifukwa anthu amene ankakhala mʼdzikolo inu musanafike ankachita zinthu zonyansa zimenezi,+ ndipo panopa dzikolo ndi lodetsedwa. 28 Mukapewa kuchita zimenezi, dziko silidzakulavulani chifukwa cholidetsa ngati mmene lidzalavulire mitundu imene ikukhalamo inu musanafike. 29 Aliyense wa inu akadzachita chilichonse cha zinthu zonyansazi, adzaphedwa kuti asadzakhalenso pakati pa anthu ake. 30 Choncho muzisunga malamulo anga popewa kuchita miyambo yonyansa iliyonse imene anthu akhala akuchita inu musanafike,+ kuti musadzidetse ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
19 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza gulu lonse la Aisiraeli kuti, ‘Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.+
3 Aliyense wa inu azilemekeza* mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 4 Musatsatire milungu yopanda pake+ kapena kudzipangira milungu yachitsulo chosungunula.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5 Mukamapereka nsembe yamgwirizano kwa Yehova,+ muziipereka mʼnjira yakuti Mulungu asangalale nanu.+ 6 Muzidya nyama yoperekedwa nsembeyo pa tsiku limene mwaipereka ndiponso tsiku lotsatira, koma yotsala mpaka tsiku lachitatu muziiwotcha pamoto.+ 7 Ngati munthu wadya nyamayo pa tsiku lachitatu, wadya nyama yonyansa. Mulungu sadzalandira nsembe imeneyo. 8 Munthu amene wadya nyamayo aziyankha mlandu wa kulakwa kwakeko chifukwa waipitsa chinthu chopatulika cha Yehova. Munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.
9 Mukamakolola zinthu zamʼmunda mwanu, musamachotseretu zonse mʼmphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha* mʼmunda mwanumo.+ 10 Komanso, musamakolole mphesa zotsala zamʼmunda mwanu kapena kutola mphesa zimene zamwazika mʼmunda mwanu. Zimenezo muzisiyira anthu osauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11 Musamabe,+ musamapusitse anzanu+ ndiponso musamachitirane chinyengo. 12 Musamalumbire zabodza mʼdzina langa+ nʼkuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. 13 Musamabere anzanu mwachinyengo+ ndipo musamalande zinthu za aliyense.+ Malipiro a munthu waganyu asagone mʼnyumba mwanu mpaka mʼmawa.+
14 Musamatemberere* munthu amene ali ndi vuto losamva ndipo munthu amene ali ndi vuto losaona musamamuikire chinthu chopunthwitsa.+ Muziopa Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova.
15 Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka kapena munthu wolemera.+ Ndipo muziweruza mwachilungamo.
16 Usamayendeyende pakati pa anthu a mtundu wako nʼkumafalitsa miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.*+ Ine ndine Yehova.
17 Usamadane ndi mʼbale wako mumtima mwako,+ koma uzimudzudzula+ kuti iwenso usakhale wochimwa ngati iyeyo.
18 Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu a mtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova.
19 Malamulo angawa muziwasunga: Musamachititse kuti ziweto zanu zamitundu yosiyana zikwerane. Podzala mbewu mʼmunda mwanu musamasakanize mitundu iwiri yosiyana.+ Ndipo musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.*+
20 Mwamuna akagona ndi kapolo wamkazi amene mbuye wake anamulonjeza kuti adzamupereka kwa mwamuna wina, koma mkaziyo sanawomboledwe kapena kupatsidwa ufulu, pazikhala chilango. Koma iwo asaphedwe chifukwa mkaziyo anali asanakhale mfulu. 21 Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula pakhomo la chihema chokumanako.+ 22 Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Azichita zimenezi popereka kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula ija ndipo munthuyo adzakhululukidwa tchimo lakelo.
23 Mukafika mʼdziko limene mukupita nʼkudzala mtengo uliwonse wa zipatso, zipatso zake zizikhala zodetsedwa kwa inu ndipo mtengowo musamauyandikire. Musamayandikire mtengowo kwa zaka zitatu ndipo musamadye zipatso zake. 24 Koma mʼchaka cha 4, zipatso zake zonse zizikhala zoyera ndipo muzizipereka kwa Yehova mosangalala.+ 25 Ndiyeno mʼchaka cha 5, mungathe kukolola zipatso zake mofanana ndi mbewu zina zonse komanso kudya zipatso za mtengowo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
26 Musamadye chilichonse chimene chili ndi magazi.+
Musamaombeze kapena kuchita zamatsenga.+
27 Musamamete ndevu zanu zotsikira mʼmasaya kapena kudula nsonga za ndevu zanu.*+
28 Musamadzicheke chifukwa cha munthu wakufa,+ ndipo musamadzilembe zizindikiro pakhungu lanu. Ine ndine Yehova.
29 Musamanyoze mwana wanu wamkazi pomupangitsa kuti akhale hule,+ kuopera kuti dziko lingachite uhule nʼkudzaza ndi makhalidwe otayirira.+
30 Muzisunga masabata anga+ ndipo muzilemekeza* malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
31 Musamapemphe anthu olankhula ndi mizimu+ kuti akuthandizeni ndipo musamafunse malangizo kwa anthu olosera zamʼtsogolo+ nʼkukuchititsani kukhala odetsedwa. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
32 Anthu aimvi uziwagwadira,+ munthu wachikulire uzimupatsa ulemu+ ndipo uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova.
33 Ngati munthu akukhala mʼdziko lanu monga mlendo, musamamuchitire zoipa.+ 34 Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa.+ Muzimukonda ngati mmene mumadzikondera nokha, chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
35 Musamachite chinyengo poyeza kutalika kwa chinthu, kulemera kwa chinthu kapena poyeza kuchuluka kwa zinthu.+ 36 Muzikhala ndi masikelo olondola, miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu ndi miyezo yolondola.*+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo. 37 Muzisunga malamulo anga onse ndi zigamulo zanga zonse, ndipo muzizitsatira.+ Ine ndine Yehova.’”
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu aliyense wa Chiisiraeli ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli amene wapereka mwana wake aliyense kwa Moleki, aziphedwa ndithu.+ Nzika zamʼdziko lanu zizimupha pomuponya miyala. 3 Ine ndidzamukana munthu ameneyo ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake, chifukwa wapereka mwana wake kwa Moleki ndipo wadetsa malo anga oyera+ komanso waipitsa dzina langa loyera. 4 Koma nzikazo zikanyalanyaza mwadala zimene munthuyo wachita popereka mwana wake kwa Moleki ndipo iwo sanamuphe,+ 5 ineyo ndidzadana ndi munthu ameneyo limodzi ndi banja lake.+ Ndidzapha munthu ameneyu limodzi ndi onse ogwirizana naye pochita uhule ndi Moleki, kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.
6 Munthu amene wachita zosakhulupirika* podalira anthu olankhulana ndi mizimu+ komanso olosera zamʼtsogolo,+ ndidzadana naye ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+
7 Choncho mudzipatule ndipo mukhale oyera,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8 Muzisunga malamulo anga ndipo muziwatsatira.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani kuti mukhale oyera.+
9 Munthu akatemberera* bambo kapena mayi ake, aziphedwa ndithu.+ Mlandu wa magazi ake ukhale pa iye chifukwa watemberera bambo ake kapena mayi ake.
10 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wachita chigololo ndi mkazi wa munthu wina: Mwamuna amene wachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake aziphedwa ndithu. Mwamuna ndi mkazi amene achita chigololowo onse aziphedwa.+ 11 Mwamuna amene wagona ndi mkazi wa bambo ake, wachititsa manyazi* bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo. 12 Mwamuna akagona ndi mpongozi wake wamkazi, onse awiri aziphedwa ndithu. Iwo achita zinthu zosemphana ndi chibadwa. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.+
13 Mwamuna akagona ndi mwamuna mnzake ngati mmene mwamuna amagonera ndi mkazi, onse awiri achita chinthu chonyansa.+ Iwo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.
14 Mwamuna akakwatira mkazi nʼkugonanso ndi mayi a mkaziyo, limenelo ndi khalidwe lonyansa.*+ Mwamunayo ndi akazi onsewo* aziphedwa kenako nʼkuwawotcha+ kuti anthu asapitirize kuchita khalidwe lonyansalo.
15 Mwamuna akagona ndi nyama, aziphedwa ndithu ndipo muziphanso nyamayo.+ 16 Mkazi akadzipereka kwa nyama kuti agone nayo,+ muzipha mkaziyo ndi nyamayo. Anthu ochita zimenezi aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.
17 Mwamuna akagona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Choncho onse awiri aziphedwa pamaso pa anthu a mtundu wawo. Iye wachititsa manyazi* mchemwali wake ndipo aziyankha mlandu wa kulakwa kwakeko.
18 Mwamuna akagona ndi mkazi amene akusamba, onse awiri sanalemekeze magazi a mkaziyo.+ Onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wawo.
19 Usagone ndi mchemwali wa mayi ako kapena mchemwali wa bambo ako, chifukwa kuchita zimenezo nʼkuchititsa manyazi mʼbale wako.+ Iwo aziyankha mlandu wa kulakwa kwawo. 20 Ndipo mwamuna amene wagona ndi mkazi wa mchimwene wa bambo ake, wachititsa manyazi* mchimwene wa bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziyankha mlandu wa tchimo lawolo. Iwo ayenera kufa kuti asabereke ana. 21 Mwamuna akakwatira mkazi wa mchimwene wake, wachita chinthu chonyansa.+ Iye wachititsa manyazi* mchimwene wake. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kufa kuti asabereke ana.
22 Muzisunga+ malamulo anga onse ndi zigamulo zanga zonse,+ kuti dziko limene ndikukulowetsani kuti mukhalemo lisadzakulavuleni.+ 23 Musamatsatire malamulo a mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ 24 Nʼchifukwa chake ndinakuuzani kuti: “Inuyo mudzatenga dzikolo ndipo ine ndidzalipereka mʼmanja mwanu kuti likhale lanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndakupatulani kwa anthu a mitundu ina.”+ 25 Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse ndi nyama, mbalame kapena chilichonse chokwawa padziko lapansi chimene ndanena kuti ndi chodetsedwa.+ 26 Mukhale oyera kwa ine, chifukwa ine Yehova ndine woyera.+ Ine ndikukusiyanitsani ndi anthu a mitundu ina kuti mukhale anthu anga.+
27 Mwamuna kapena mkazi aliyense amene amalankhula ndi mizimu kapena kulosera zamʼtsogolo* aziphedwa ndithu.+ Aziphedwa powaponya miyala. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.’”
21 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Uza ansembe, ana a Aroni kuti, ‘Aliyense wa inu asadzidetse chifukwa cha munthu amene wamwalira pakati pa anthu a mtundu wake.+ 2 Koma angathe kudzidetsa ngati wamwalirayo ndi wachibale wake wapafupi, mayi ake, bambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi ndi mchimwene wake. 3 Angathenso kudzidetsa ngati wamwalirayo ndi mchemwali wake, amene ndi namwali wosakwatiwa yemwe amakhala naye limodzi. 4 Koma sakuyenera kudzidetsa chifukwa cha mkazi wamwini pakati pa anthu a mtundu wake nʼkudziipitsa. 5 Asamamete mpala mitu yawo,+ asamamete ndevu zamʼmasaya mwawo ndipo asamadzitemeteme thupi lawo.+ 6 Azikhala oyera kwa Mulungu wawo+ ndipo asamadetse dzina la Mulungu wawo,+ chifukwa iwowa amapereka kwa Yehova nsembe zowotcha pamoto, zomwe ndi chakudya cha Mulungu wawo, choncho azikhala oyera.+ 7 Wansembe asamakwatire hule+ kapena mkazi amene wataya unamwali wake. Asamakwatirenso mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati,+ chifukwa wansembeyo ndi woyera kwa Mulungu wake. 8 Muzimuona kuti ndi woyera+ chifukwa ndi amene amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu, chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+
9 Mwana wamkazi wa wansembe akadzidetsa pochita uhule, ndiye kuti akudetsa bambo ake. Aziphedwa kenako nʼkumuwotcha.+
10 Mkulu wa ansembe wokhala pakati pa abale ake ansembe, amene anamuthira mafuta odzozera unsembe pamutu pake,+ nʼkuikidwa kukhala wansembe* kuti azivala zovala zaunsembe,+ asalekerere tsitsi lake osalisamala ndipo asangʼambe zovala zake.+ 11 Iye asayandikire munthu aliyense wakufa+ ndipo asamadzidetse ngakhale amene wamwalirayo atakhala bambo ake kapena mayi ake. 12 Asamatuluke mʼmalo opatulika ndipo asamadetse malo opatulika a Mulungu wake,+ chifukwa pamutu pake pali chizindikiro cha kudzipereka, chomwe ndi mafuta odzozera a Mulungu wake.+ Ine ndine Yehova.
13 Mkulu wa ansembe akafuna kukwatira, azikwatira namwali.+ 14 Asakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati, mkazi amene wataya unamwali wake kapena hule, koma azikwatira namwali pakati pa anthu amtundu wake. 15 Asadetse ana ake* pakati pa anthu a mtundu wake,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndamuyeretsa.’”
16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17 “Lankhula ndi Aroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana ako,* ku mibadwo yawo yonse, amene ali ndi chilema asayandikire malo opatulika kudzapereka chakudya cha Mulungu wake. 18 Munthu akakhala ndi chilema chilichonse, asayandikire malo opatulika. Kaya akhale ndi vuto losaona, wolumala, wankhope yopotoka,* wamkono kapena mwendo wautali kwambiri kuposa unzake, 19 wothyoka phazi kapena dzanja, 20 wa linunda, wamfupi kwambiri,* wa diso lolumala, wa zikanga, wa zipere ndi wa mavalo owonongeka.+ 21 Munthu aliyense mwa ana a Aroni* wansembe, amene ali ndi chilema, asamayandikire guwa lansembe kudzapereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Asamayandikire guwa lansembe kudzapereka chakudya cha Mulungu wake chifukwa ali ndi chilema. 22 Iye angathe kudya chakudya cha Mulungu wake kuchokera pa zinthu zopatulika koposa+ ndi pa zinthu zopatulika.+ 23 Koma asamayandikire katani+ ndiponso guwa lansembe,+ chifukwa iye ali ndi chilema. Asadetse malo anga opatulika,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa.’”+
24 Choncho Mose anafotokoza zimenezi kwa Aroni ndi ana ake, ndiponso kwa Aisiraeli onse.
22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aroni ndi ana ake kuti azilemekeza* zinthu zopatulika zimene Aisiraeli abweretsa kwa ine,+ kuti asadetse dzina langa loyera.+ Ine ndine Yehova. 3 Uwauze kuti, ‘Mʼmibadwo yanu yonse munthu aliyense wodetsedwa mwa ana anu, amene wakhudza zinthu zopatulika zimene Aisiraeli azipatula kuti azipereke nsembe kwa Yehova, munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pamaso panga.+ Ine ndine Yehova. 4 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni amene ali ndi khate+ kapena nthenda yakukha,+ asadye zinthu zopatulika mpaka atakhala woyera.+ Zikhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wokhudza munthu amene wadetsedwa chifukwa cha munthu wakufa,+ kapena mwamuna amene watulutsa umuna,+ 5 kapenanso mwamuna amene wakhudza chilichonse mwa zamoyo zodetsedwa zopezeka zambiri,+ kapena amene wakhudza munthu wodetsedwa pa chifukwa chilichonse amene angachititse kuti akhale wodetsedwa.+ 6 Munthu wokhudza chilichonse mwa zinthu zoterezi azikhala wodetsedwa mpaka madzulo ndipo asamadye chinthu chopatulika chilichonse, koma azisamba thupi lonse.+ 7 Dzuwa likalowa adzakhalanso woyera, ndipo pambuyo pake akhoza kudya zina mwa zinthu zopatulika, chifukwa ndi chakudya chake.+ 8 Sakuyeneranso kudya nyama iliyonse imene waipeza yakufa kapena imene yaphedwa ndi zilombo nʼkukhala wodetsedwa.+ Ine ndine Yehova.
9 Iwo azisunga malamulo anga kuti asachimwe nʼkufa chifukwa chodetsa zinthu zopatulika atalephera kusunga malamulowo. Ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa.
10 Munthu wamba* asadye chinthu chopatulika chilichonse.+ Mlendo wokhala mʼnyumba ya wansembe kapena munthu waganyu, asadye chinthu chopatulika chilichonse. 11 Koma ngati wansembe wagula munthu ndi ndalama zake, munthuyo angathe kudya nawo zinthu zopatulikazo. Akapolo obadwira mʼnyumba ya wansembe, angathenso kudya nawo chakudya chake.+ 12 Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi munthu amene si wansembe,* asamadye nawo zopereka zopatulika. 13 Koma mwana wa wansembe akakhala mkazi wamasiye kapena ngati anasiyidwa ukwati alibe mwana aliyense, ndipo wabwerera kunyumba kwa bambo ake kumene anali ali mwana, angathe kudya nawo chakudya cha bambo ake.+ Koma munthu wamba* asamadye nawo.
14 Munthu akadya mosadziwa chinthu chopatulika, azibweza chinthucho nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a chinthucho. Azipereka chinthu chopatulikacho kwa wansembe.+ 15 Zili choncho kuti ansembe asamadetse zinthu zopatulika za Aisiraeli, zimene amapereka kwa Yehova,+ 16 nʼkuchititsa anthuwo kuti achimwe nʼkulandira chilango chifukwa chakuti adya zinthu zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndikuwayeretsa.’”
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18 “Uza Aroni ndi ana ake komanso Aisiraeli onse kuti, ‘Mwamuna aliyense amene ndi wa Chiisiraeli kapena mlendo wokhala mu Isiraeli amene akupereka kwa Yehova nsembe yopsereza+ pofuna kukwaniritsa malonjezo ake kapena kuti ikhale nsembe yake yaufulu,+ 19 azipereka nyama yopanda chilema,+ ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo kapena mbuzi, kuti Mulungu asangalale naye. 20 Musamapereke nsembe nyama iliyonse yachilema,+ chifukwa Mulungu sangasangalale nanu.
21 Ngati munthu akupereka nsembe yamgwirizano+ kwa Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, azipereka ngʼombe kapena nkhosa yopanda chilema, kuti Mulungu ailandire. Izikhala yopanda chilema chilichonse. 22 Isakhale yakhungu, yothyoka fupa, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo* kapena zipere. Musamapereke kwa Yehova nyama zoterezi kapena kuwotcha nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova. 23 Mungapereke ngʼombe kapena nkhosa yomwe ili ndi mwendo wautali kwambiri kapena waufupi kwambiri kuposa unzake kuti ikhale nsembe yaufulu. Koma Mulungu sadzailandira ngati mukuipereka ngati nsembe pokwaniritsa lonjezo lanu. 24 Musamapereke kwa Yehova nyama imene mavalo ake ndi owonongeka, ophwanyika kapena yofulidwa. Musamapereke nsembe nyama zoterezi mʼdziko lanu. 25 Ndipo nyama iliyonse mwa nyama zoterezi imene mlendo wakupatsani musamaipereke nsembe kuti ikhale chakudya cha Mulungu wanu, chifukwa ili ndi chilema ndipo Mulungu sadzailandira.’”
26 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27 “Ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, izikhala ndi mayi ake masiku 7,+ koma kuyambira tsiku la 8 kupita mʼtsogolo mungaipereke kwa Yehova monga nsembe yowotcha pamoto, ndipo Mulungu adzailandira. 28 Musamaphe ngʼombe kapena nkhosa ndi mwana wake pa tsiku limodzi.+
29 Mukafuna kupereka nsembe yoyamikira kwa Yehova+ muziipereka mʼnjira yakuti Mulungu asangalale nanu. 30 Muziidya tsiku lomwelo. Musasiye nyama iliyonse mpaka mʼmamawa.+ Ine ndine Yehova.
31 Muzisunga malamulo anga komanso kuwatsatira.+ Ine ndine Yehova. 32 Musamadetse dzina langa loyera,+ mʼmalomwake muzindiona kuti ndine wopatulika pakati pa Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova amene ndikukuyeretsani.+ 33 Ndine amene ndakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova.”
23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Muzilengeza+ zikondwerero+ za Yehova zimene ndi misonkhano yopatulika. Izi ndi zikondwerero zanga:
3 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Limeneli ndi tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse chifukwa limeneli ndi sabata la Yehova kulikonse kumene mungakhale.+
4 Zikondwerero za Yehova, kapena kuti misonkhano yopatulika imene muyenera kulengeza pa nthawi yake yoikidwiratu ndi iyi: 5 Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la Pasika wa Yehova.+
6 Pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, muzichitira Yehova Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ 7 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika+ ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. 8 Kwa masiku 7, muzipereka kwa Yehova nsembe zowotcha pamoto. Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.’”
9 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mukadzalowa mʼdziko limene ndikukupatsani, nʼkukolola mbewu zamʼdzikomo, muzidzabweretsa kwa wansembe+ mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+ 11 Ndipo wansembe azidzayendetsa mtolowo uku ndi uku pamaso pa Yehova kuti Mulungu asangalale nanu. Sabata likatha, wansembe azidzayendetsa mtolowo uku ndi uku pa tsiku lotsatira. 12 Pa tsiku loyendetsa mtolo wanu uku ndi uku, muzipereka mwana wa nkhosa wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, kuti akhale nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova. 13 Popereka nsembe imeneyi muziperekanso nsembe yambewu. Nsembeyo izikhala ufa wosalala wothira mafuta, muyezo wake magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.* Muziperekanso vinyo wa nsembe yachakumwa, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.* 14 Musamadye mkate, mbewu zokazinga kapena mbewu zatsopano mpaka tsiku limeneli litafika komanso mutabweretsa nsembe ya Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale.
15 Kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata, pamene munabweretsa mtolo kuti ukhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku,+ muziwerenga masabata 7, ndipo sabata iliyonse izikhala ndi masiku okwanira. 16 Muziwerenga masiku 50+ kukafika pa tsiku lotsatizana ndi tsiku limene Sabata la 7 lathera, kenako muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova.+ 17 Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate wamʼnyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Poiphika izikhala ndi zofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+ 18 Popereka mitanda ya mkateyi muziperekanso ana a nkhosa amphongo opanda chilema okwana 7, aliyense wa chaka chimodzi, komanso ngʼombe imodzi yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.+ Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe yopsereza, nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. Ziziperekedwa pamodzi ndi nsembe yambewu ndi nsembe zachakumwa kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 19 Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo,+ ndi ana a nkhosa amphongo awiri, aliyense wachaka chimodzi, monga nsembe yamgwirizano.+ 20 Wansembe aziyendetsa uku ndi uku ana a nkhosa awiriwo pamodzi ndi mitanda ya mkate ya zipatso zoyambirira kucha, monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi zizikhala zinthu zopatulika kwa Yehova ndipo zizikhala za wansembe.+ 21 Pa tsiku limeneli muzilengeza+ kuti kuli msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kulikonse kumene mungakhale mʼmibadwo yanu yonse.
22 Mukamakolola zinthu zamʼmunda mwanu, musamachotseretu zonse mʼmphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha mʼmunda mwanumo.+ Zotsalazo muzisiyira wosauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 24 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mʼmwezi wa 7, pa tsiku loyamba la mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, ndipo lipenga likalira+ muzisonkhana kuti mulambire Mulungu. 25 Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli, ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova.’”
26 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27 “Tsiku la 10 mʼmwezi wa 7 umenewu, ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni*+ chifukwa cha machimo anu ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. 28 Pa tsiku limeneli musamagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sadzasonyeza kuti akudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo ake pa tsiku limeneli adzaphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 30 Munthu aliyense wogwira ntchito iliyonse pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga nʼkumuchotsa pakati pa anthu a mtundu wake. 31 Musamagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 32 Ili ndi sabata lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni+ chifukwa cha machimo anu madzulo pa tsiku la 9 la mweziwo. Muzisunga sabata kuyambira madzulo mpaka madzulo tsiku lotsatira.”
33 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 34 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Tsiku la 15 la mwezi wa 7 umenewu, ndi tsiku lochitira Yehova Chikondwerero cha Misasa kwa masiku 7.+ 35 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. 36 Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.
37 Zimenezi ndi zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza monga misonkhano yopatulika+ yoperekera nsembe zowotcha pamoto kwa Yehova. Imeneyi ndi misonkhano yoperekera nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ motsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku. 38 Muzichita zimenezi kuwonjezera pa zimene mumapereka pa masabata a Yehova,+ mphatso zanu,+ nsembe zanu zimene mumapereka pokwaniritsa lonjezo+ ndi nsembe zanu zonse zaufulu+ zimene mukuyenera kupereka kwa Yehova. 39 Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7, mukakolola zinthu zamʼmunda mwanu, muzichita chikondwerero cha Yehova masiku 7.+ Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi tsiku lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzipumanso pa ntchito zanu zonse pa tsiku la 8.+ 40 Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi yamʼchigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ 41 Muzichitira Yehova chikondwerero chimenechi kwa masiku 7 pa chaka,+ mʼmwezi wa 7. Limeneli ndi lamulo mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 42 Muzikhala mʼmisasa masiku 7.+ Mbadwa zonse za Isiraeli zizikhala mʼmisasa, 43 kuti mibadwo yanu ya mʼtsogolo idzadziwe+ kuti ine ndinachititsa Aisiraeli kukhala mʼmisasa powatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
44 Choncho Mose anafotokozera Aisiraeli za zikondwerero za Yehova.
24 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 3 Aroni azikhazika nyale kunja kwa katani ya Malo Oyera Koposa mʼchihema chokumanako. Nyalezo ziziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka mʼmawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse. 4 Nyalezo azikhazike pachoikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, ndipo zizikhala pamaso pa Yehova nthawi zonse.
5 Utenge ufa wosalala nʼkuphika mikate 12 yozungulira yoboola pakati. Mkate uliwonse uzipangidwa ndi ufa wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* 6 Ndipo usanjikize mikateyo mʼmagulu awiri. Gulu lililonse likhale ndi mikate 6.+ Uike mikateyo patebulo lagolide woyenga bwino pamaso pa Yehova.+ 7 Pagulu lililonse la mikateyo uike lubani weniweni. Lubaniyo aziperekedwa nsembe yowotcha pamoto+ kwa Yehova kuimira nsembe yonseyo. 8 Pa tsiku lililonse la Sabata azikhazika mkatewo pamaso pa Yehova nthawi zonse.+ Limeneli ndi pangano pakati pa ine ndi Aisiraeli mpaka kalekale. 9 Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera mʼmalo oyera,+ chifukwa waperekedwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.”
10 Ndiyeno panali mnyamata wina amene mayi ake anali a Chiisiraeli, koma bambo ake anali a ku Iguputo.+ Mnyamatayu anayamba kumenyana ndi munthu wina wa Chiisiraeli mumsasa. 11 Mnyamatayo anayamba kunyoza* ndi kutukwana dzina la Mulungu.*+ Ndiye anapita naye kwa Mose.+ Dzina la mayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri wa fuko la Dani. 12 Ndiyeno anamutsekera kudikira kuti Yehova apereke chigamulo pa nkhaniyo.+
13 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 14 “Munthu wotemberera dzina la Mulungu uja, mupite naye kunja kwa msasa. Onse amene anamumva akutemberera aike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse limuponye miyala.+ 15 Ndiyeno uuze Aisiraeli kuti, ‘Ngati munthu aliyense watemberera Mulungu wake, aziyankha mlandu wa tchimo lakelo. 16 Choncho munthu amene wanyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Gulu lonse lizimuponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo.
17 Munthu aliyense amene wapha munthu, nayenso aziphedwa ndithu.+ 18 Munthu amene wamenya nʼkupha chiweto cha mnzake, azibweza chiweto china, chiweto kulipira chiweto.* 19 Munthu akavulaza mnzake, zimene wachitira mnzakezo iyenso muzimʼchitira zomwezo.+ 20 Kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Mmene wavulazira mnzake nayenso muzimʼvulaza chimodzimodzi.+ 21 Munthu amene wamenya nʼkupha chiweto cha mnzake azilipira,+ koma amene wamenya nʼkupha munthu nayenso aziphedwa.+
22 Chigamulo chilichonse chizigwira ntchito mofanana kwa mlendo wokhala pakati panu ndi kwa nzika,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
23 Kenako Mose anafotokoza zimenezi kwa Aisiraeli, ndipo iwo anatulutsa munthu wotemberera uja kunja kwa msasa nʼkumuponya miyala.+ Choncho Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
25 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose paphiri la Sinai kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsani,+ dzikolo lizikasunga sabata la Yehova.+ 3 Kwa zaka 6 muzikalima minda yanu, ndipo pa zaka 6 zimenezo muzidzadulira mitengo yanu ya mpesa ndi kukolola mbewu zanu.+ 4 Koma mʼchaka cha 7 dzikolo lizidzasunga sabata lopuma pa zonse, sabata la Yehova. Musamadzadzale mbewu mʼminda yanu kapena kudulira mitengo yanu ya mpesa. 5 Musamadzakolole mbewu zomera zokha kuchokera pa mbewu zimene munakolola chaka chapita, ndipo musamadzakololenso mphesa za mʼmitengo yanu yosadulirayo. Chaka chimenecho dziko lizidzapuma pa zonse. 6 Koma mungathe kudya chakudya chimene chamera mʼmunda mwanu mʼchaka cha sabatacho. Inuyo, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, waganyu wanu ndi alendo amene akukhala mʼnyumba mwanu mungathe kudya. 7 Zimene zamerazo zikhalenso chakudya cha ziweto zanu ndi zilombo zakutchire. Mbewu zonse zomera zokha zikhale chakudya.
8 Muzidzawerenga masabata 7 azaka, zaka 7 kuchulukitsa maulendo 7. Nthawi yonse ya masabata 7 azaka izidzakwana zaka 49. 9 Ndiyeno mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzidzaliza lipenga la nyanga ya nkhosa mokweza kwambiri. Pa Tsiku Lochita Mwambo Wophimba Machimo,+ muzidzaliza lipengalo kuti limveke mʼdziko lanu lonse. 10 Chaka cha 50 chizidzakhala chopatulika ndipo muzidzalengeza ufulu kwa anthu onse okhala mʼdzikolo.+ Chizikhala Chaka cha Ufulu kwa inu, ndipo aliyense azibwerera kumalo ake ndi kubanja lake.+ 11 Chaka cha 50 chidzakhala Chaka cha Ufulu kwa inu. Musadzalime minda yanu kapena kukolola mbewu zomera zokha, kapenanso kukolola mphesa zamʼmitengo yosadulira.+ 12 Chimenecho ndi Chaka cha Ufulu ndipo chizikhala chopatulika kwa inu. Zimene mungathe kudya ndi zimene zamera zokha mʼminda yanu.+
13 MʼChaka cha Ufulu chimenechi, aliyense wa inu azibwerera kumalo ake.+ 14 Mukamagulitsa chinthu kwa mnzanu kapena kugula chinthu kwa mnzanu, musamachitirane chinyengo.+ 15 Ukamagula malo kwa mnzako, uziwerenga zaka zimene zadutsa kuchokera mʼChaka cha Ufulu. Azikugulitsa malowo mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti udzalepo mbewu.+ 16 Ngati patsala zaka zambiri, angathe kukweza mtengo wogulitsira malowo, koma ngati patsala zaka zochepa, azitsitsa mtengo wa malowo, chifukwa akukugulitsa kuchuluka kwa mbewu zimene udzakolole. 17 Pasapezeke aliyense pakati panu wochitira mnzake chinyengo,+ ndipo muziopa Mulungu wanu,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 18 Mukamasunga malamulo anga komanso kutsatira zigamulo zanga mudzakhala otetezeka mʼdzikolo.+ 19 Dzikolo lidzakupatsani zipatso zake.+ Mudzadya ndi kukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mmenemo.+
20 Koma ngati munganene kuti: “Popeza sitidzalima minda yathu nʼkukolola mbewu zathu, tidzadya chiyani mʼchaka cha 7?”+ 21 Dziwani kuti ndidzakudalitsani mʼchaka cha 6, ndipo dzikolo lidzakupatsani chakudya chokwanira zaka zitatu.+ 22 Kenako mudzadzala mbewu mʼchaka cha 8, ndipo mudzapitiriza kudya chakudya chimene munakolola chija mpaka mʼchaka cha 9. Mudzadya chakalecho mpaka mutakololanso china.
23 Musamagulitsiretu malo anu mpaka kalekale+ chifukwa dzikolo ndi langa.+ Kwa ine, inu ndinu alendo mʼdziko langa.+ 24 Mʼdziko lanu lonselo, munthu azikhala ndi ufulu wogulanso malo ake.
25 Mʼbale wanu akasauka nʼkugulitsa ena mwa malo ake, womuwombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene mʼbale wakeyo anagulitsa.+ 26 Ngati munthu alibe womuwombola, koma walemera nʼkukhala ndi ndalama zowombolera malo ake, 27 aziwerenga zaka zimene zadutsa kuchokera pamene anagulitsa malowo, ndipo azibweza ndalama zotsala kwa munthu amene anagula malowo. Akatero azibwerera kumalo akewo.+
28 Koma ngati munthu amene anagulitsa malo sanapeze ndalama zoti angabwezere kwa amene anagulayo, malo amene anagulitsawo apitirizebe kukhala a munthu amene anawagulayo mpaka Chaka cha Ufulu chitafika.+ Mʼchaka chimenecho malowo azibwezedwa kwa mwiniwake ndipo amene anagulitsa maloyo azibwerera kumalo akewo.+
29 Munthu akagulitsa nyumba mumzinda wokhala ndi mpanda, azikhala ndi ufulu woiwombola+ chaka chimodzi chisanathe kuchokera pamene anaigulitsa. Azikhala ndi ufulu umenewu kwa chaka chathunthu. 30 Koma ngati sanaiwombole chaka chimodzicho chisanathe, nyumba imene ili mumzinda wokhala ndi mpanda izikhala ya amene anagulayo mpaka kalekale, mʼmibadwo yake yonse, ndipo isamabwezedwe mʼChaka cha Ufulu. 31 Koma nyumba zimene zili mʼmidzi yopanda mpanda zizitengedwa monga mbali ya munda wa kunja kwa mzinda. Ufulu woiwombola uzikhalapobe, ndipo mʼChaka cha Ufulu izibwezedwa kwa mwiniwake.
32 Koma nyumba za Alevi zimene zili mʼmizinda yawo,+ Aleviwo azikhala ndi ufulu woziwombola mpaka kalekale. 33 Ndipo ngati Mlevi anagulitsa nyumba mumzinda wawo ndipo sanaiwombole, izibwezedwa kwa Mleviyo mʼChaka cha Ufulu.+ Zizikhala choncho chifukwa nyumba zamʼmizinda ya Alevi pakati pa Aisiraeli ndi za Aleviwo basi.+ 34 Komanso, asagulitse malo odyetserako ziweto+ ozungulira mizinda yawo, chifukwa amenewo ndi malo awo mpaka kalekale.
35 Mʼbale wanu akasauka pakati panu ndipo sangathe kudzisamalira, muzimuthandiza+ ngati mmene mungathandizire mlendo wokhala pakati panu,+ kuti nayenso akhale ndi moyo. 36 Musamalandire chiwongoladzanja kapena kupezerapo phindu+ pa iye.* Muziopa Mulungu wanu+ ndipo mʼbale wanu azikhala ndi moyo pakati panu. 37 Mukamukongoza ndalama musamafunepo chiwongoladzanja+ kapena kumupatsa chakudya kuti mupezerepo phindu. 38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+ kuti ndikupatseni dziko la Kanani. Ndinachita izi kuti ndikusonyezeni kuti ine ndine Mulungu wanu.+
39 Mʼbale wanu amene mukukhala naye pafupi akasauka nʼkudzigulitsa kwa inu,+ musamamugwiritse ntchito ngati kapolo.+ 40 Muzimuona ngati waganyu+ komanso ngati mlendo. Azikugwirirani ntchito mpaka Chaka cha Ufulu. 41 Mʼchaka chimenecho iye ndi ana ake* azichoka nʼkubwerera kwa achibale ake. Azibwerera kumalo a makolo ake.+ 42 Aisiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Choncho asamadzigulitse ngati mmene anthu amagulitsira kapolo. 43 Musamamuchitire nkhanza,+ ndipo muziopa Mulungu wanu.+ 44 Akapolo anu aamuna ndi aakazi azichokera mʼmitundu yokuzungulirani. Muzigula kapolo wamwamuna kapena wamkazi kuchokera mʼmitundu imeneyi. 45 Komanso muzigula akapolo kuchokera kwa ana a alendo okhala pakati panu.+ Mungagule akapolo kuchokera kwa iwo ndi kwa ana amene alendowo abereka mʼdziko lanu. Amenewa muziwagula kuti akhale akapolo anu. 46 Akapolowa mungathe kusiyira ana anu monga cholowa chawo mpaka kalekale. Anthu amenewa ndi amene azikhala antchito anu, koma Aisiraeli, omwe ndi abale anu musamawachitire nkhanza.+
47 Koma ngati mlendo wokhala pakati panu walemera, ndipo mʼbale wanu amene akukhala naye pafupi wasauka nʼkudzigulitsa kwa mlendoyo, kapena kwa munthu wina wa mʼbanja la mlendoyo, 48 mʼbale wanuyo azikhalabe ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola.+ 49 Komanso mchimwene wa bambo ake, mwana wa mchimwene wa bambo akewo, wachibale wake aliyense wapafupi, kapena kuti aliyense wa mʼbanja lake angathe kumuwombola.
Kapenanso mwiniwakeyo akalemera, azidziwombola.+ 50 Kuti achite zimenezi, iye aziwerengera limodzi ndi amene anamugulayo nthawi imene yadutsa kuchokera chaka chimene anadzigulitsa kudzafika Chaka cha Ufulu.+ Ndalama zimene anamugulira zizigwirizana ndi kuchuluka kwa zakazo.+ Malipiro a ntchito imene azigwira pa nthawi yotsalayo azifanana ndi a waganyu.+ 51 Ngati kwatsala zaka zochuluka, ndalama zake zodziwombolera zizigwirizana ndi zaka zimene zatsala. 52 Koma ngati kwatsala zaka zochepa kuti Chaka cha Ufulu chifike, aziwerenga yekha zaka zotsalazo, ndipo azipereka ndalama zodziwombolera zogwirizana ndi zaka zotsalazo. 53 Azimugwirira ntchito mofanana ndi waganyu chaka ndi chaka ndipo muzionetsetsa kuti sakumuchitira nkhanza.+ 54 Koma ngati sangathe kudziwombola potsatira njira zimenezi, adzachoka mʼChaka cha Ufulu,+ iye pamodzi ndi ana ake.*
55 Chifukwa Aisiraeli ndi akapolo anga. Iwo ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
26 “‘Musapange milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika kuti muzichilambira. Musaike mwala wogoba+ mʼdziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 2 Muzisunga masabata anga ndipo muzilemekeza* malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
3 Mukapitiriza kutsatira malangizo anga ndi kusunga malamulo anga,+ 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo yamʼmunda idzakupatsani zipatso zake. 5 Mudzakhala mukupuntha zimene mwakolola mpaka kufika nyengo yokolola mphesa, ndipo mudzakhala mukukolola mphesa mpaka kufika nyengo yofesa mbewu. Mudzadya mkate wanu nʼkukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mʼdziko lanu.+ 6 Ndidzakupatsani mtendere mʼdzikolo,+ moti mudzagona pansi popanda wokuopsezani.+ Ndidzachotsa zilombo zoopsa zakutchire mʼdziko lanu, ndipo palibe amene adzachite nanu nkhondo. 7 Mudzathamangitsa adani anu ndi kuwagonjetsa ndi lupanga. 8 Anthu anu 5 adzathamangitsa adani 100, ndipo anthu 100 adzathamangitsa adani 10,000, moti mudzagonjetsa adani anu ndi lupanga.+
9 Ndidzakudalitsani,* kukuchititsani kuti mubereke ana ambiri komanso kukuchulukitsani.+ Ndipo ndidzasunga pangano langa ndi inu.+ 10 Pamene mukudya chakudya cha chaka chapita, mudzafunika kuchitulutsa kuti mupeze malo oikapo chatsopano. 11 Ine ndidzaika chihema changa pakati panu,+ ndipo sindidzakukanani. 12 Ine ndidzayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu,+ inuyo mudzakhala anthu anga.+ 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti musakhale akapolo a Aiguputo. Ndinathyola goli lanu ndi kukuchititsani kuyenda mowongoka.*
14 Koma ngati simudzandimvera kapena kutsatira malamulo onsewa,+ 15 ndipo mukadzakana malangizo anga,+ nʼkunyansidwa ndi zigamulo zanga mpaka kukana kutsatira malamulo anga onse, nʼkufika pophwanya pangano langa,+ 16 ine ndidzakuchitani zotsatirazi: Ndidzakulangani pokupangitsani kukhala ndi mantha, kudwala chifuwa chachikulu ndi kutentha kwa thupi koopsa, zimene zidzachititsa maso anu khungu ndi kukufooketsani. Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+ 17 Ine ndidzakukanani, ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+
18 Koma ngati simudzandimverabe pambuyo poona zinthu zimenezi, ndidzakulangani kuchulukitsa maulendo 7 kuposa poyamba chifukwa cha machimo anu. 19 Ndidzakuchititsani kuti musiye kunyada ndipo ndidzachititsa kumwamba kukhala ngati chitsulo+ ndi nthaka yanu ngati kopa.* 20 Mphamvu zanu zidzathera pachabe, chifukwa nthaka yanu siidzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo yamʼmunda mwanu siidzakupatsani zipatso.
21 Koma mukapitirizabe kuchita zosemphana ndi zofuna zanga, osafuna kundimvera, ndidzakulangani kuchulukitsa maulendo 7 mogwirizana ndi machimo anu. 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu nʼkuchepetsa chiwerengero chanu, moti mʼmisewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+
23 Ngati pambuyo pa zimenezi simudzasintha+ nʼkupitirizabe kuyenda motsutsana ndi ine, 24 inenso ndidzatsutsana nanu, ndipo ndidzakulangani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu. 25 Ndidzabweretsa lupanga lobwezera chilango pa inu chifukwa chophwanya pangano.+ Mukadzathawira mʼmizinda yanu, ndidzabweretsa matenda pakati panu+ ndipo mudzaperekedwa mʼdzanja la mdani.+ 26 Ndikadzawononga njira* zanu zopezera chakudya,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi wokha, ndipo pokugawirani mkatewo, adzachita kukuyezerani+ nʼkukupatsani wochepa. Choncho mudzadya koma simudzakhuta.+
27 Koma ngati pambuyo pa zonsezi simudzandimvera, nʼkupitirizabe kuyenda motsutsana ndi ine, 28 inenso ndidzatsutsana nanu koopsa,+ ndipo ineyo ndidzakukwapulani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu. 29 Choncho mudzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ 30 Ndidzawononga malo anu opatulika olambirirako+ ndipo ndidzagwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaunjika mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo ndidzachoka pakati panu monyansidwa.+ 31 Mizinda yanu ndidzaiwononga+ ndi lupanga ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu, komanso sindidzalandira nsembe zanu za kafungo kosangalatsa.* 32 Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja,+ ndipo adani anu amene azidzakhala mʼdzikolo adzaliyangʼanitsitsa modabwa.+ 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukuthamangitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja, ndipo mizinda yanu idzawonongedwa.+
34 Pa masiku onse amene dzikolo lidzakhale bwinja, lidzabweza masabata ake, inu muli mʼdziko la adani anu. Nthawi imeneyo, dziko lidzapuma* chifukwa likuyenera kubweza masabata ake.+ 35 Masiku onse amene dzikolo lidzakhale bwinja lidzakhala likupuma, chifukwa silinapume, pa nthawi imene munkayenera kusunga masabata anu mukukhala mʼdzikolo.
36 Ndidzaika mantha mʼmitima ya anthu amene adzapulumuke+ omwe akukhala mʼdziko la adani awo, moti adzathawa phokoso la tsamba louluka. Iwo adzathawa ngati munthu amene akuthawa lupanga, moti adzagwa popanda wowathamangitsa.+ 37 Iwo adzagwetsana okhaokha ngati anthu amene akuthawa lupanga, koma popanda munthu wowathamangitsa. Simudzatha nʼkomwe kulimbana ndi adani anu.+ 38 Ambiri mwa inu mudzafa mʼdziko la anthu a mitundu ina,+ ndipo dziko la adani anu lidzakumezani. 39 Anthu amene adzatsale pakati panu adzazunzika mʼmayiko a adani awo+ chifukwa cha zolakwa zanu. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo.+ 40 Kenako adzavomereza zolakwa zawo+ komanso kusakhulupirika ndi zolakwa za makolo awo. Ndipo adzavomereza kuti anachita zinthu mosakhulupirika poyenda motsutsana nane.+ 41 Atatero, inenso ndinayenda motsutsana nawo+ ndipo ndinawapititsa kudziko la adani awo.+
Izi zinachitika kuti mwina mitima yawo yosadulidwayo ingadzichepetse+ nʼkulipira chifukwa cha zolakwa zawo. 42 Choncho ndidzakumbukira pangano limene ndinachita ndi Yakobo,+ Isaki+ komanso Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pa nthawi imene iwo anasiya kukhala mʼdzikomo, dzikolo linkabweza masabata ake+ ndipo linakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo anapereka malipiro a zolakwa zawo, chifukwa anakana zigamulo zanga ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+ 44 Koma ngakhale kuti padzachitika zonsezi, iwo akamadzakhala mʼdziko la adani awo, sindidzawakana mpaka kalekale+ kapena kunyansidwa nawo moti nʼkuwawonongeratu, zomwe zingaphwanye pangano langa+ ndi iwo, chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Ndipo kuti zinthu ziwayendere bwino ndidzakumbukira pangano limene ndinachita ndi makolo awo+ amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo, anthu a mitundu ina akuona.+ Ndidzachita zimenezi kuti ndiwasonyeze kuti ndine Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”
46 Amenewa ndi malangizo, zigamulo komanso malamulo amene Yehova anakhazikitsa pakati pa iye ndi Aisiraeli mʼphiri la Sinai, kudzera mwa Mose.+
27 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu akapanga lonjezo lapadera+ lopereka munthu mnzake kwa Yehova pa mtengo womwe unaikidwa, 3 ndipo ngati munthu amene akuperekedwayo ndi wamwamuna, wazaka zapakati pa 20 ndi 60, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli* asiliva 50, pamuyezo wofanana ndi sekeli yakumalo oyera.* 4 Koma ngati munthuyo ndi wamkazi, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 30. 5 Ndipo ngati munthu amene akuperekedwayo ndi wazaka zapakati pa 5 ndi 20, akakhala wamwamuna mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 20, koma akakhala wamkazi mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 10. 6 Ngati munthuyo ndi woyambira mwezi umodzi kufika zaka 5, akakhala wamwamuna mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli asiliva 5, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli asiliva atatu.
7 Ndiyeno ngati zaka za munthu amene akuperekedwayo ndi zoyambira pa 60 kupita mʼtsogolo, akakhala wamwamuna, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 15, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli 10. 8 Koma ngati munthu amene akulonjezayo ndi wosauka moti sangakwanitse mtengo womwe unaikidwawo,+ azikaonetsa munthuyo kwa wansembe, ndipo wansembe azinena mtengo wake. Wansembe adzanena mtengo umene munthu amene analonjezayo angakwanitse.+
9 Koma ngati walonjeza kupereka nyama yomwe ndi yoyenera kuperekedwa nsembe kwa Yehova, nyama iliyonse imene angapereke kwa Yehova izikhala yopatulika. 10 Asaichotse nʼkuikapo ina, ndipo asasinthanitse yabwino ndi yoipa kapena yoipa ndi yabwino. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndiponso imene waisinthanitsayo, zizikhala zopatulika. 11 Koma ngati akupereka nyama yodetsedwa+ imene sikuyenera kuperekedwa nsembe kwa Yehova, azikaonetsa nyamayo kwa wansembe. 12 Wansembe azinena mtengo wake mogwirizana ndi mmene nyamayo ilili, kaya ndi yabwino kapena yoipa. Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 13 Koma ngati akufuna kuiwombola, azipereka mtengo wa nyamayo womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.+
14 Munthu akapereka nyumba yake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, wansembe aziiona nʼkunena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyumbayo ilili, kaya ndi yabwino kapena ayi. Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo.+ 15 Koma amene wapereka nyumbayo akafuna kuiwombola, azipereka mtengo wa nyumbayo womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo. Akatero nyumbayo izikhala yake.
16 Ngati munthu wapereka mbali ina ya munda wake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angadzalepo. Ngati angadzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri,* ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50. 17 Ngati wapereka mundawo kuyambira mʼChaka cha Ufulu+ kupita mʼtsogolo, mtengo wake womwe unaikidwa uzikhala womwewo. 18 Koma ngati akupereka mundawo Chaka cha Ufulu chitadutsa, wansembe azimuwerengera mtengo wake mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kukafika mʼChaka cha Ufulu chotsatira, ndipo azichotsera pa mtengo wake womwe unaikidwa.+ 19 Koma ngati munthu amene anapereka mundayo akufuna kuuwombola, azipereka mtengo wake womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake 5, akatero mundawo uzikhala wake. 20 Ngati mundawo sanauwombole ndipo wagulitsidwa kwa munthu wina, sangathenso kuuwombola. 21 Mundawo ukamadzabwezedwa mʼChaka cha Ufulu, udzakhala wopatulika kwa Yehova monga munda umene waperekedwa kwa iye. Mundawo udzakhala wa ansembe.+
22 Ngati munthu wapereka munda kwa Yehova kuti ukhale wopatulika, koma mundawo anachita kugula ndipo sunali mbali ya cholowa chake,+ 23 wansembe azimuwerengera mtengo wake, mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti Chaka cha Ufulu chifike, ndipo tsiku lomwelo azipereka mtengo umene wansembe wawerengerawo.+ Ndalamazo ndi zopatulika kwa Yehova. 24 MʼChaka cha Ufulu mundawo udzabwezedwa kwa mwiniwake weniweni amene anaugulitsa.+
25 Mtengo uliwonse womwe unaikidwa uzikhala wofanana ndi sekeli yakumalo oyera. Sekeli imodzi izikwana magera* 20.
26 Koma munthu asapereke nyama iliyonse yoyamba kubadwa kuti ikhale yopatulika, chifukwa iliyonse yoyamba kubadwa ndi ya Yehova.+ Kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, ndi za Yehova.+ 27 Koma ngati ndi nyama yodetsedwa ndipo waiwombola mogwirizana ndi mtengo womwe unaikidwa, azipereka mtengo wa nyamayo nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.+ Koma ngati sangaiwombole izigulitsidwa pa mtengo womwe unaikidwa.
28 Koma zinthu zimene munthu wapereka kwa Yehova monga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kuchokera pa katundu wake, sizikuyenera kugulitsidwa kapena kuwomboledwa, kaya ndi munthu, nyama kapena munda. Chinthu chilichonse chimene munthu wapereka kwa Yehova ndi chopatulika koposa.+ 29 Kuwonjezera pamenepa, munthu aliyense amene waperekedwa kwa Mulungu kuti awonongedwe sangathe kuwomboledwa.+ Ameneyo aziphedwa ndithu.+
30 Chakhumi chilichonse+ cha zinthu zamʼdzikolo, kaya ndi zokolola zamʼmunda kapena zipatso zamʼmitengo, ndi za Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova. 31 Ngati munthu akufuna kuwombola chakhumi chake chilichonse, azipereka mtengo wa chakhumicho nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo. 32 Ngʼombe kapena nkhosa iliyonse ya 10, pa nyama zonse zodutsa pansi pa ndodo ya mʼbusa, nyama iliyonse ya 10 izikhala yopatulika kwa Yehova. 33 Asaifufuze ngati ili yabwino kapena yoipa, ndiponso asaisinthanitse ndi ina. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndi imene waisinthanitsayo, zizikhala zopatulika.+ Sangathe kuiwombola.’”
34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anapatsa Mose paphiri la Sinai+ kuti apereke kwa Aisiraeli.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Kapena kuti, “mafuta okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “mafuta ake okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
“Kudula” kumeneku ankadula ndi zikhadabo ndipo sankachotseratu mutu.
Kapena kuti, “phulusa lamafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Zikuoneka kuti uchi umenewu sunali wa njuchi koma anali madzi azipatso, chifukwa ukutchulidwa kuti zipatso zoyambirira. (Le 2:12; 2Mb 31:5)
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “muzipereka tirigu wamuwisi.”
Kapena kuti, “nsembe yamtendere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate,” kutanthauza chakudya cha Mulungu chochokera pansembe yamgwirizano.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate,” kutanthauza chakudya cha Mulungu chochokera pansembe yamgwirizano.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “phulusa lamafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Nʼkutheka kuti akunena akulu amene ankaimira khamu lonselo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Akamva mawu otemberera (lumbiro).” Nʼkutheka kuti chinali chilengezo chokhudza tchimo chimene ankatchulanso mawu otemberera munthu wochimwayo kapena mboni imene ikudziwa za nkhaniyo ngati italephera kudzapereka umboni wake.
Apa zikuonetsa kuti munthuyo sanakwaniritse zimene analumbira.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
Kapena kuti, “zovala zamkati zobisa.”
Kapena kuti, “phulusa la mafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “chamkuwa.”
Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”
Kapena kuti, “mafuta okuta impso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “a fuko lako.”
Kapena kuti, “Nyama zapamtunda.”
Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.
Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “khate” amatanthauza zambiri kuphatikizapo matenda apakhungu osiyanasiyana opatsirana. Angaphatikizenso matenda ena opezeka mʼzovala ndi mʼnyumba.
Sankafunikanso kumuika kwayekha kwa masiku 7 ngati mmene ankachitira nthawi zonse, kuti atsimikizire ngati ali ndi khate kapena ayi, chifukwa zinali zodziwikiratu kuti munthuyo ali ndi khate.
Kapena kuti, “azigamula kuti nthendayo sangapatsire ena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ili mu ulusi wowombera nsalu woyenda mulitali kapena mulifupi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi ofanana ndi malita 6.6. Onani Zakumapeto B14.
“Muyezo umodzi” umenewu ndi wofanana ndi malita 0.31. Onani Zakumapeto B14.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.
Kapena kuti, “zovala zamʼkati zobisa.”
Kapena kuti, “a fuko lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuzi ya Azazeli.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene dzanja lake lidzadzazidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “zimene akuchita nazo uhule.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti amuvule.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuvula bambo ako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Usavule mchimwene wa bambo ako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuvula.”
Kapena kuti, “khalidwe lochititsa manyazi.”
Kapena kuti, “aperekedwe nsembe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aziopa.”
Kapena kuti, “musamatenge zotsala.”
Kapena kuti, “ovutika.”
Kapena kuti, “Musamafunire zoipa.”
Mabaibulo ena amati, “Usamangoyangʼana pamene moyo wa mʼbale wako uli pangozi.”
Kutanthauza chovala chimene nsalu yake anaiwomba mophatikiza ulusi wathonje ndi ubweya wankhosa. Onani De 22:11.
Apa akuwaletsa kuchita zimene anthu akunja ankachita, koma sakutanthauza kuti asamayepule ndevu zawo ngakhale pangʼono.
Mʼchilankhulo choyambirira, “muziopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Muzikhala ndi muyezo wolondola wa efa komanso muyezo wolondola wa hini.” Muyezo wa efa ankaugwiritsa ntchito poyeza zinthu zouma ngati tirigu, koma muyezo wa hini ankaugwiritsa ntchito poyeza zinthu zamadzi. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “amene wachita uhule ndi milungu ina.”
Kapena kuti, “akafunira zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula.”
Kapena kuti, “khalidwe lochititsa manyazi.”
Zimenezi zikhoza kusonyeza kuti akazi onsewo anavomereza khalidwe lochititsa manyazilo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula.”
Kapena kuti, “kapena amene ali ndi mzimu wolosera zamʼtsogolo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkudzaza dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wamphuno yokhadzuka.”
Mabaibulo ena amati, “munthu woonda kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya Aroni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzipatule pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Kapena kuti, “akakwatiwa ndi mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14
Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “wovutika.”
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mabaibulo ena amati, “amene sakusala kudya.”
Kapena kuti, “yamʼkhwawa.”
Magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 4.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kutemberera.”
Pamenepa akutanthauza dzina lakuti Yehova mogwirizana ndi vesi 15 ndi 16.
Kapena kuti, “moyo kulipira moyo.”
Kapena kuti, “kumupatsa ngongole yakatapira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana ake aamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana ake aamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muziopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakucheukirani.”
Kapena kuti, “kuyenda mutakweza mitu.”
Kutanthauza kuti mvula siidzagwa kuchokera kumwamba ndipo nthaka idzakhala youma.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndodo.” Nʼkutheka kuti akutanthauza ndodo zimene ankazigwiritsira ntchito posunga mkate.
Mawu a Chiheberi angatanthauzenso “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito pofotokoza chinthu chimene munthu akunyansidwa nacho.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “lidzasunga sabata.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Gera limodzi linali lofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.