Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Deuteronomy 1:1-34:12
  • Deuteronomo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Deuteronomo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Deuteronomo

Deuteronomo

1 Awa ndiwo mawu amene Mose analankhula ndi Aisiraeli onse m’chipululu, m’chigawo cha Yorodano,+ m’chipululu moyang’anana ndi Sufu, pakati pa Parana,+ Tofeli, Labani, Hazeroti+ ndi Dizahabi, 2 mtunda woyenda masiku 11 kuchokera ku Horebe kudzera njira ya kuphiri la Seiri yopita ku Kadesi-barinea.+ 3 Ndiyeno m’chaka cha 40,*+ m’mwezi wa 11, pa tsiku loyamba la mweziwo, Mose analankhula ndi ana a Isiraeli zonse zimene Yehova anamulamula kuti awauze. 4 Apa n’kuti atagonjetsa Sihoni+ mfumu ya Aamori imene inali kukhala ku Hesiboni. Anali atagonjetsanso Ogi+ mfumu ya Basana imene inali kukhala ku Asitaroti.+ Mfumu imeneyi anaigonjetsera ku Edirei.+ 5 Mose anayamba kufotokoza chilamulo ichi+ m’chigawo cha Yorodano m’dziko la Mowabu, kuti:

6 “Yehova Mulungu wathu anatilankhula tili ku Horebe,+ kuti, ‘Mwakhalitsa m’dera lino lamapiri.+ 7 Tembenukani ndi kulowera kudera lamapiri la Aamori+ ndi anthu oyandikana nawo onse okhala ku Araba,+ kudera lamapiri,+ ku Sefela, ku Negebu,+ m’mbali mwa nyanja,+ m’dziko la Akanani+ ndi ku Lebanoni+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+ 8 Taonani, ndikukupatsani dzikolo. Mukalowe m’dzikolo ndi kulitenga kuti likhale lanu, dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abulahamu, Isaki+ ndi Yakobo,+ kuti adzalipereka kwa iwo ndi kwa mbewu yawo.’+

9 “Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani kuti, ‘Ndekha sindikwanitsa kusenza mtolo wokutsogolerani.+ 10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ndipo onani lero mwachulukadi ngati nyenyezi zakuthambo.+ 11 Yehova Mulungu wa makolo anu achulukitse chiwerengero chanu+ pochiwirikiza kambirimbiri, ndipo akudalitsenidi+ mmene anakulonjezerani.+ 12 Inuyo ndinu mtolo ndi katundu wolemera. Ndingathe bwanji ndekha kukusenzani, ndi mikangano yanuyo?+ 13 Sankhani amuna anzeru, aluso+ ndi ozindikira+ m’mafuko anu, kuti ndiwaike kukhala atsogoleri anu.’+ 14 Pamenepo munandiyankha kuti, ‘Zimene mwatiuza kuti tichitezi n’zabwino.’ 15 Choncho ndinatenga atsogoleri a mafuko anu, amuna anzeru ndi ozindikira n’kuwaika kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50, atsogoleri a magulu a anthu 10, ndi akapitawo a m’mafuko anu.+

16 “Pa nthawi imeneyo ndinalamula oweruza anu kuti, ‘Mukamazenga mlandu wa pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi m’bale wake, kapena ndi mlendo wokhala m’nyumba mwake.+ 17 Musamakondere poweruza.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope munthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu.+ Mlandu umene wakuvutani muziubweretsa kwa ine kuti ndiumve.’+ 18 Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani zonse zimene muyenera kuchita.

19 “Kenako tinachoka ku Horebe ndi kuyenda kudutsa chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha chonse chija+ chimene munachiona, podzera njira ya m’dera lamapiri la Aamori,+ monga momwe Yehova Mulungu wathu anatilamulira, mpaka tinafika ku Kadesi-barinea.+ 20 Ndiyeno ndinakuuzani kuti, ‘Mwafika m’dera lamapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.+ 21 Onani, Yehova Mulungu wanu wakusiyirani dzikoli.+ Pitani, litengeni kuti likhale lanu, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakuuzirani.+ Musaope kapena kuchita mantha.’+

22 “Koma nonsenu munabwera kwa ine ndi kunena kuti, ‘Tiloleni titumize amuna, atsogole kukationera dzikolo ndipo adzatiuze njira imene tiyenera kudzera ndiponso mizinda imene tikapeze kumeneko.’+ 23 Pamenepo, ndinaona kuti amenewo ndi maganizo abwino, moti ndinatenga amuna 12 pakati panu, mmodzi m’fuko lililonse.+ 24 Choncho iwo ananyamuka ndi kupita kulowa m’dera lamapiri.+ Anayenda mpaka anafika m’chigwa* cha Esikolo,+ ndipo anazonda dzikolo. 25 Motero anatengako zina mwa zipatso za m’dzikolo+ ndi kutibweretsera. Iwo anatiuza kuti, ‘Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.’+ 26 Koma inu simunafune kupita kukalowa m’dzikolo,+ ndipo munayamba kupandukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.+ 27 Pamenepo munapitiriza kung’ung’udza m’mahema mwanu kuti, ‘Yehova anatitulutsa m’dziko la Iguputo+ chifukwa chodana nafe,+ kuti adzatipereke m’manja mwa Aamori kuti atiwononge.+ 28 Tipite kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu+ potiuza kuti: “Kumeneko tinaonako anthu akuluakulu, ndiponso aatali kuposa ifeyo,+ ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ Kumeneko tinaonakonso ana a Anaki.”’+

29 “Ndiye ine ndinakuuzani kuti, ‘Musachite mantha kapena kuwaopa.+ 30 Yehova Mulungu wanu ndiye akukutsogolerani. Adzakumenyerani nkhondo+ mofanana ndi zonse zimene anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona,+ 31 komanso m’chipululu,+ kumene munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani.+ M’njira yonse imene munayenda anakunyamulani ngati mmene bambo amanyamulira mwana wake, mpaka kufika malo ano.’+ 32 Ngakhale kuti munamva mawu amenewa, simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,+ 33 amene anali kutsogola kuti akuzondereni malo oti mumangepo msasa wanu.+ Usiku anali kukutsogolerani ndi moto kuti muziona njira yoyendamo, ndipo masana anali kukutsogolerani ndi mtambo.+

34 “Nthawi yonseyi Yehova anali kumvetsera mawu anu. Motero anakwiya kwambiri, ndipo analumbira+ kuti, 35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a m’badwo woipa uwu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune.+ Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzagawira dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+ 37 (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, ‘Iwenso sukalowamo.+ 38 Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira ndi amene akalowamo.’+ Mulungu wamulimbitsa+ chifukwa ndi amene adzatsogolere ana a Isiraeli pokalandira dzikolo.) 39 Koma ana anu amene munanena kuti: “Adzagwidwa ndi adani!”+ ndiponso ana anu aang’ono amene lero sakudziwa chabwino kapena choipa, amenewa ndiwo adzalowa m’dziko limenelo. Amenewa ndidzawapatsa dzikolo ndipo adzalitenga kukhala lawo. 40 Koma inu, sinthani njira ndipo muyambe kulowera kuchipululu, kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.’+

41 “Pamenepo munayankha ndi kundiuza kuti, ‘Tachimwira Yehova.+ Ife tipitadi kukamenya nkhondo mogwirizana ndi zonse zimene Yehova Mulungu wathu watilamula!’ Choncho aliyense wa inu anamanga m’chiuno zida zake zankhondo, ndipo munaona ngati n’zosavuta kukwera m’phirimo.+ 42 Koma Yehova anandiuza kuti, ‘Auze kuti: “Musakwere kukamenya nkhondo, chifukwa ine sindili pakati panu.+ Chifukwa mukapita mudzagonjetsedwa ndi adani anu.”’+ 43 Motero ine ndinalankhula nanu, ndipo simunamvere koma munayamba kupandukira+ lamulo la Yehova ndi kuchita zinthu modzikuza, motero munanyamuka kupita m’phiri.+ 44 Kumeneko Aamori okhala m’phiri limenelo anatuluka kudzakumana nanu ndipo anakuthamangitsani,+ mmene njuchi zimachitira, ndi kukubalalitsani m’phiri la Seiri mpaka kukafika ku Horima.+ 45 Zitatero munabwerera ndi kuyamba kulira pamaso pa Yehova, koma Yehova sanamve mawu anu+ ndipo sanakutchereni khutu.+ 46 Chotero munakhala ku Kadesi masiku ambiri.+

2 “Ndiyeno tinatembenuka ndi kulowera kuchipululu kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anandiuzira.+ Ndipo tinayenda masiku ambiri m’dera lapafupi ndi phiri la Seiri. 2 Kenako Yehova anandiuza kuti, 3 ‘Mwayenda kwa nthawi yaitali m’dera lapafupi ndi phirili.+ Tembenukani ndi kulowera kumpoto. 4 Auze anthuwo kuti: “Mukudutsa m’malire a dziko la abale anu,+ ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri.+ Iwo adzachita nanu mantha,+ choncho muyenera kukhala osamala kwambiri. 5 Musalimbane nawo, chifukwa sindikupatsani dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha. Ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+ 6 Mudzadya chakudya chimene mudzagula kwa iwo ndi ndalama, ndipo mudzamwa madzi amene mudzagula kwa iwo ndi ndalama.+ 7 Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene dzanja lanu likuchita.+ Iye akudziwa za kuyenda kwanu kudutsa m’chipululu chachikulu ichi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi,+ ndipo simunasowe kanthu.”’+ 8 Chotero tinalambalala abale athu, ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba,+ Elati ndi Ezioni-geberi.+

“Kenako tinatembenuka ndi kudutsa njira ya m’chipululu cha Mowabu.+ 9 Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Usavutitse Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari+ kwa ana a Loti kuti akhale malo awo.+ 10 (Kale munali kukhala Aemi,+ anthu amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Iwo anali ataliatali ngati Aanaki.+ 11 Arefai+ anali kuonedwanso ngati Aanaki,+ ndipo Amowabu anali kutcha Arefaiwo kuti Aemi. 12 Kale Ahori+ anali kukhala m’Seiri, ndipo ana a Esau+ anawalanda dzikolo ndi kuwapha. Atatero, ana a Esauwo anayamba kukhala m’dzikolo,+ monga mmene ana a Isiraeli ayenera kuchitira m’dziko lawo, limene Yehova adzawapatsa ndithu.) 13 Choncho nyamukani ndi kudutsa chigwa* cha Zeredi.’ Pamenepo tinadutsadi chigwa cha Zeredi.+ 14 Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-barinea mpaka kuwoloka chigwa cha Zeredi anali zaka 38, kufikira m’badwo wa amuna otha kupita kunkhondo utatha pakati panu, monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo.+ 15 Dzanja+ la Yehova linali pa iwo kuwasautsa ndi kuwachotsa pakati panu, kufikira onse atatha.+

16 “Ndiyeno amuna onse otha kupita kunkhondo atatha kufa pakati pa anthu,+ 17 Yehova analankhulanso ndi ine, kuti, 18 ‘Lero udutsa m’dera la Mowabu, pafupi ndi Ari,+ 19 ndipo uyandikire pafupi ndi ana a Amoni. Usawavutitse kapena kumenyana nawo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko la ana a Amoni kuti likhale lako. Dziko limeneli ndinalipereka kwa ana a Loti kuti likhale lawo.+ 20 Dzikoli linali kudziwika kuti ndi la Arefai.+ (Kale munali kukhala Arefai ndipo Aamoni anali kutcha Arefaiwo kuti Azamuzumi. 21 Anthu amenewa anali amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Analinso ataliatali ngati Aanaki.+ Yehova anawafafaniza+ kuwachotsa pamaso pa ana a Amoni kuti ana a Amoniwo atenge dzikolo ndi kukhalamo, 22 monga mmene anachitira ndi ana a Esau amene akukhala m’Seiri.+ Iye anafafaniza Ahori+ kuwachotsa pamaso pa ana a Esau, kuti ana a Esauwo atenge dzikolo ndi kukhalamo mpaka lero. 23 Aavi+ amene anali kukhala m’midzi mpaka kukafika ku Gaza,+ anawonongedwa ndi Akafitori+ ochokera ku Kafitori,+ kuwachotsa pamaso pawo kuti Akafitoriwo akhale m’dzikolo.)

24 “‘Nyamukani, muyende ndi kudutsa chigwa cha Arinoni.+ Taonani, ndapereka m’manja mwanu Sihoni,+ Mwamori, mfumu ya Hesiboni. Yambani kulanda dziko lake, ndipo menyanani naye nkhondo. 25 Lero ndichititsa anthu a mitundu ina okhala pansi pa thambo, amene adzamva za inu, kuchita nanu mantha kwambiri ndi kuyamba kukuopani. Chifukwa cha inu, iwo adzanthunthumira ndi kumva zopweteka zofanana ndi zowawa za pobereka.’+

26 “Kenako, ndinatumiza amithenga a mawu amtendere+ kuchokera m’chipululu cha Kademoti,+ kupita kwa Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, kuti, 27 ‘Ndilole ndidutse m’dziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu. Sindidzatembenukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 28 Ndidzadya chakudya chimene udzandigulitsa ndi ndalama, ndipo ndidzamwa madzi amene udzandigulitsa ndi ndalama. Ndilole ndingodutsa m’dziko lako,+ 29 monga mmene ana a Esau amene akukhala m’Seiri+ ndi Amowabu+ amene akukhala mu Ari anachitira kwa ine. Ndidzadutsa m’dziko lako mpaka kukawoloka Yorodano, kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa.’+ 30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+

31 “Zitatero, Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndikupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+ 32 Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33 Yehova Mulungu wathu anam’pereka kwa ife,+ ndipo tinam’gonjetsa+ limodzi ndi ana ake ndi anthu ake onse. 34 Tinalandanso mizinda yake yonse pa nthawi imeneyo ndi kuwononga mzinda wina uliwonse.+ Tinapha amuna, akazi ndi ana, ndipo sitinasiye munthu aliyense wamoyo. 35 Ziweto zokha n’zimene tinatenga monga zofunkha pamodzi ndi zofunkha za m’mizinda imene tinalanda.+ 36 Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso kuchokera kumzinda wa m’chigwa mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda womwe unali wa malinga aatali kwambiri kwa ife.+ Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife. 37 Koma simunayandikire dziko la ana a Amoni,+ dera lonse la m’mbali mwa chigwa cha Yaboki,+ kapena mizinda ya m’dera lamapiri, kapenanso malo alionse amene Yehova Mulungu wathu sanatilamule kuti tiwalande.

3 “Ndiyeno tinatembenuka ndi kulowera njira ya ku Basana. Pamenepo, Ogi+ mfumu ya Basana inatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe nkhondo ku Edirei.+ 2 Chotero Yehova anandiuza kuti, ‘Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndim’pereka ndithu m’manja mwako. Ndim’pereka pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake. Umuchite zimene unachitira Sihoni+ mfumu ya Aamori, amene anali kukhala m’Hesiboni.’ 3 Pamenepo Yehova Mulungu wathu anaperekanso Ogi mfumu ya Basana ndi anthu ake onse m’manja mwathu, ndipo tinam’kantha moti sipanatsale ndi mmodzi yemwe wopulumuka mwa anthu ake.+ 4 Pa nthawi imeneyo tinalanda mizinda yake yonse. Panalibe mzinda umene sitinawalande. Tinalanda mizinda 60+ m’chigawo chonse cha Arigobi,+ m’dera lonse la ufumu wa Ogi ku Basana.+ 5 Mizinda yonseyi inali ya mipanda yolimba kwambiri ndiponso yaitali, yokhala ndi zitseko ndi mipiringidzo. Kuwonjezera pamenepo, tinalandanso matauni ambirimbiri akumidzi. 6 Yonseyo tinaiwononga,+ monga mmene tinachitira ndi Sihoni mfumu ya Hesiboni, mwa kuwononga mzinda uliwonse, amuna, akazi ndi ana aang’ono.+ 7 Ndipo tinatenga ziweto ndi zofunkha zonse za m’mizindayo.+

8 “Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko m’manja mwa mafumu awiri amenewo a Aamori+ amene anali kukhala m’dera la Yorodano, kuyambira m’chigwa* cha Arinoni+ mpaka kuphiri la Herimoni.+ 9 (Asidoni anali kutcha phiri la Herimoni kuti Sirioni,+ pamene Aamori anali kulitcha kuti Seniri.)+ 10 Tinalanda mizinda yonse ya kudera lokwererapo, m’Giliyadi monse, m’Basana monse, mpaka ku Saleka+ ndi ku Edirei,+ mizinda ya m’dera la ufumu wa Ogi ku Basana. 11 Mwa Arefai+ onse, Ogi yekha mfumu ya Basana ndi amene anali atatsala. Chithatha chimene anaikapo mtembo wake chinali chachitsulo. Kodi si chija chili ku Raba+ wa ana a Aamoni? N’chachitali mikono* 9, ndipo m’lifupi mwake mikono inayi, kutsatira muyezo wodziwika. 12 Choncho pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu. Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa Aroweli,+ mzinda umene uli m’chigwa cha Arinoni, ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi, ndi mizinda yake. 13 Hafu ya fuko la Manase ndinalipatsa dera lotsala la Giliyadi+ ndi Basana+ yense wa ufumu wa Ogi. Kodi si paja dera lonse la Arigobi+ limene ndi Basana yense, limatchedwa dziko la Arefai?+

14 “Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri+ ndi a Amaakati,+ ndipo midzi ya ku Basana imeneyo anaitcha dzina la iye mwini lakuti, Havoti-yairi*+ kufikira lero. 15 Makiri+ ndinam’patsa Giliyadi.+ 16 Mafuko a Rubeni+ ndi Gadi ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi+ kukafika kuchigwa cha Arinoni, ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a ana a Amoni.+ 17 Ndinawapatsa Araba, Yorodano ndi tsidya lake la kum’mawa, kuchokera ku Kinereti*+ mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere+ imene ili m’munsi mwa Pisiga,+ kotulukira dzuwa.

18 “Chotero ndinakulamulani pa nthawi imeneyo kuti, ‘Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli kuti mulitenge kukhala lanu. Amuna nonse olimba mtima muwoloke, mukuyenda patsogolo pa abale anu, ana a Isiraeli, muli okonzeka ndi zida.+ 19 Akazi anu okha ndi ana anu aang’ono ndiwo atsale m’mizinda yanu imene ndakupatsani.+ Ziweto zanunso zitsale (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri), 20 kufikira Yehova atapatsa abale anu ndi inu nomwe mpumulo, ndiponso kufikira iwo atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akulipereka kwa iwo tsidya linalo la Yorodano. Mukatero mudzabwerera, aliyense kumalo ake amene ndakupatsani.’+

21 “Pa nthawi imeneyo ndinalamula Yoswa+ kuti, ‘Iwe ukuona ndi maso zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita ndi mafumu awiriwa. Yehova adzachitanso chimodzimodzi ndi maufumu onse amene ali kumene mukuwolokera.+ 22 Amuna inu, musawaope amenewo, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo.’+

23 “Pa nthawi imeneyo ndinam’chonderera Yehova kuti atikomere mtima, ndipo ndinati, 24 ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndinu amene mwayamba kuchititsa atumiki anu kuti aone ukulu wanu+ ndi dzanja lanu lamphamvu.+ Ndi mulungu winanso uti, kumwamba kapena padziko lapansi, amene akuchita ntchito ngati zanu, ndiponso ntchito zamphamvu ngati zanu?+ 25 Ndiloleni chonde ndiwoloke, kuti ndione dziko labwino+ limene lili kutsidya kwa Yorodano, dera lamapiri labwinoli+ ndi Lebanoni.’+ 26 Pamenepo Yehova anapitiriza kundikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo sanandimvere. Motero Yehova anandiuza kuti, ‘Basi khala chete! Usatchulenso nkhani imeneyi kwa ine. 27 Kwera pamwamba pa Pisiga+ ndi kukweza maso ako, ndipo uyang’ane kumadzulo, kumpoto, kum’mwera ndi kum’mawa, uone dzikolo ndi maso ako, chifukwa suwoloka Yorodano uyu.+ 28 Uike Yoswa kukhala mtsogoleri+ ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa+ anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.’+ 29 Zonsezi zinachitika tili m’chigwa moyang’anana ndi Beti-peori.+

4 “Tsopano inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuphunzitsani kuti muzitsatira. Mukatero mudzakhala ndi moyo+ n’kukalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani, ndi kukalitenga kukhala lanu. 2 Musawonjezepo kalikonse pa mawu amene ndikukulamulani, ndipo musachotsepo kalikonse pa mawu amenewa,+ kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.

3 “Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori, kuti munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori,+ Yehova Mulungu wanu anamuwononga ndi kum’chotsa pakati panu.+ 4 Koma nonsenu amene mukumamatira+ kwa Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo lero. 5 Taonani, ndakuphunzitsani malangizo+ ndi zigamulo,+ monga mmene Yehova Mulungu wanga wandilamulira, kuti muzikatsatira zimenezo pamene mukukhala m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu. 6 Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+ 7 Pakuti ndi mtundu winanso uti wamphamvu+ umene milungu yake ili pafupi nawo, monga mmene Yehova Mulungu wathu alili pafupi ndi ife, tikamaitanira pa iye+ nthawi zonse? 8 Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo ndi zigamulo zolungama zofanana ndi chilamulo chonsechi chimene ndikukuikirani pamaso panu lero?+

9 “Koma khalani tcheru ndipo musamale moyo wanu,+ kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona,+ ndi kuti mitima yanu isaiwale zinthu zimenezo masiku onse a moyo wanu.+ Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauza za zinthu zimenezo,+ 10 za tsiku limene munaimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe,+ pamene Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ naphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhala ndi moyo padziko, ndi kuti aphunzitsenso ana awo.’+

11 “Choncho anthu inu munayandikira ndi kuimirira m’munsi mwa phiri. Phiri limenelo linali kuyaka moto mpaka kumwamba, ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12 Pamenepo Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera pakati pa moto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu osaona kalikonse.+ 13 Pamenepo anakuuzani pangano lake,+ Mawu Khumi,*+ ndipo anakulamulani kuti muzilisunga. Kenako analemba Mawu Khumiwo pamiyala iwiri yosema.+ 14 Ndipo Yehova anandilamula pa nthawi imeneyo kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi zigamulo, kuti muzikazitsatira pamene mukukhala m’dziko limene mukuwolokerako kukalitenga.+

15 “Chotero musamale moyo wanu,+ chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse+ m’motomo. 16 Musamale kuti musachite zinthu zokuwonongetsani,+ kutinso musadzipangire chifaniziro, chifaniziro cha chinthu chilichonse, chachimuna kapena chachikazi,+ 17 chifaniziro cha nyama iliyonse ya padziko lapansi,+ chifaniziro cha mbalame iliyonse youluka m’mlengalenga,+ 18 chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene chimayenda panthaka, ndi chifaniziro cha nsomba iliyonse+ ya m’madzi a pansi pa dziko.* 19 Musamale kuti musakweze maso anu kuthambo ndi kuona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la zinthu zakuthambo, zimene Yehova Mulungu wanu wazipereka kwa anthu onse okhala pansi pa thambo lonse,+ n’kunyengeka nazo, kuzigwadira ndi kuyamba kuzitumikira.+ 20 Musachite zimenezo chifukwa Yehova ndiye anakutengani n’kukutulutsani m’ng’anjo yachitsulo,+ mu Iguputo, kuti mukhale anthu akeake+ monga mmene zilili lero.

21 “Ndipo Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu,+ kotero kuti analumbira kuti ndisawoloke Yorodano, kapena kulowa m’dziko labwino limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala cholowa chanu.+ 22 Ineyo ndifera m’dziko lino.+ Sindiwoloka Yorodano, koma inu muwoloka ndi kutenga dziko labwinoli. 23 Samalani kuti musaiwale pangano la Yehova Mulungu wanu limene anachita nanu,+ ndi kuti musadzipangire chifaniziro, chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu anakuletsani.+ 24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.*+

25 “Ukakakhala ndi ana ndi zidzukulu ndipo mwakhala nthawi yaitali m’dzikomo, n’kuchita zinthu zokuwonongetsa+ mwa kupanga chifaniziro,+ chifaniziro cha chinthu chilichonse, n’kuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ moti n’kumulakwira, 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+ 27 Ndipo Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo mudzatsala ochepa+ m’mayiko a mitundu imene Yehova adzakuingitsiraniko. 28 Kumeneko mudzatumikira milungu+ yopangidwa ndi manja a anthu, milungu ya mtengo ndi mwala,+ imene siingaone, kumva, kudya kapena kununkhiza.+

29 “Mukadzafufuza Yehova Mulungu wanu muli kumeneko, mudzam’pezadi,+ chifukwa mudzam’funafuna ndi mtima wanu wonse ndiponso moyo wanu wonse.+ 30 Pamapeto pake, mawu amenewa akadzakwaniritsidwa pa inu, n’kukhala pamavuto aakulu, mudzabwereradi kwa Yehova Mulungu wanu+ ndi kumvetsera mawu ake.+ 31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuiwala pangano+ la makolo anu limene anawalumbirira.

32 “Tafunsani tsopano, za masiku akale+ inu musanakhalepo, kuchokera pa tsiku limene Mulungu analenga munthu padziko lapansi,+ ndiponso kuchokera kumalekezero ena a thambo kukafika kumalekezero ena a thambo, Kodi chinthu chachikulu ngati chimenechi chinayamba chachitikapo, kapena kodi chinthu ngati chimenechi chinayamba chamvekapo?+ 33 Kodi anthu ena anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pakati pa moto ngati mmene inuyo munawamvera, ndi kukhalabe ndi moyo?+ 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukadzitengera mtundu wa anthu pakati pa mtundu wina ndi mayesero,+ zizindikiro,+ zozizwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula,+ ndi zoopsa zazikulu+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona? 35 Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu woona,+ ndipo palibenso wina.+ 36 Anakuchititsani kumva mawu ake kuchokera kumwamba n’cholinga chakuti akulangizeni kuti muzimumvera. Padziko lapansi pano, iye anakuchititsani kuona moto wake woopsa, ndipo munamva mawu ake kuchokera pakati pa moto.+

37 “Koma mukupitirizabe kukhala ndi moyo chifukwa anakonda makolo anu ndipo anasankha mbewu zawo zobwera pambuyo pawo,+ ndi kukutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu zake zazikulu,+ komanso anali kukuyang’anirani. 38 Anachita izi kuti achotse mitundu yaikulu ndi yamphamvu kuposa inu, ndi kulowetsamo inu, kukupatsani dziko lawo kuti likhale cholowa chanu monga mmene zilili lero.+ 39 Inu mukudziwa bwino lero, ndipo muzikumbukira m’mitima yanu, kuti Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.+ Palibenso wina.+ 40 Muzisunga malangizo+ ndi zigamulo zake zimene ndikukulamulani lero. Muzitero kuti nthawi zonse zinthu zikuyendereni bwino,+ inuyo ndi ana anu obwera pambuyo panu, ndiponso kuti mutalikitse masiku anu panthaka imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.”+

41 Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano,+ 42 kuti munthu wopha mnzake mwangozi,+ amene sanali kudana naye kale n’kale,+ azithawirako. Ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi ndi kukhala ndi moyo.+ 43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ m’chipululu cha dera lokwererapo, wothawirako Arubeni, mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, wothawirako Agadi, ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, wothawirako Amanase.+

44 Tsopano chilamulo+ chimene Mose anaika pamaso pa ana a Isiraeli ndi ichi. 45 Chilamulocho ndicho maumboni,*+ malangizo+ ndi zigamulo+ zimene Mose anauza ana a Isiraeli pamene anatuluka mu Iguputo. 46 Anawauza zimenezi ali pafupi ndi Yorodano, m’chigwa, moyang’anizana ndi Beti-peori.+ Dera limeneli ndi dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, imene inali kukhala ku Hesiboni.+ Mose ndi ana a Isiraeli anagonjetsa mfumuyi atatuluka mu Iguputo,+ 47 ndipo anamulanda dziko lakelo ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. Amenewa ndi mafumu awiri a Aamori amene anali kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano. 48 Dera limeneli linayambira ku Aroweli+ m’mphepete mwa chigwa* cha Arinoni mpaka kuphiri la Sione, limene ndi phiri la Herimoni,+ 49 ndiponso dera lonse la Araba+ m’chigawo cha kum’mawa kwa Yorodano, mpaka kunyanja ya Araba+ m’munsi mwa Pisiga.+

5 Ndiyeno Mose anaitana Aisiraeli+ onse n’kuwauza kuti: “Inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo+ zimene ndikukuuzani lero, ndipo muziphunzire ndi kuzitsatira mosamala.+ 2 Yehova Mulungu wathu anachita nafe pangano ku Horebe.+ 3 Yehova sanachite pangano limeneli ndi makolo athu, koma ndi ife, tonsefe amene tili ndi moyo pano lero. 4 Yehova analankhula nanu pamasom’pamaso m’phiri, kuchokera pakati pa moto.+ 5 Ine ndinaima pakati pa Yehova ndi inu pa nthawi imeneyo,+ kuti ndikuuzeni mawu a Yehova, (pakuti munali kuopa moto, ndipo simunakwere m’phirimo).+ Pamenepo iye anati,

6 “‘Ine ndine Yehova Mulungu wako,+ amene ndinakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 7 Usakhale ndi milungu ina iliyonse motsutsana ndi ine.+

8 “‘Usadzipangire fano+ kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cha m’madzi a pansi pa dziko lapansi.* 9 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo,* chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.+ 10 Koma ndimasonyeza kukoma mtima kosatha ku mibadwo masauzande chifukwa cha anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.+

11 “‘Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+

12 “‘Posunga tsiku la sabata ndi kuliona kukhala lopatulika, mmene Yehova Mulungu wako anakulamulira,+ 13 uzigwira ntchito zako zonse masiku 6.+ 14 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wako.+ Usagwire ntchito iliyonse,+ iweyo kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, ng’ombe yako yamphongo, bulu wako, chiweto chako chilichonse, kapena mlendo wokhala mumzinda wanu,+ kuti nayenso kapolo wako wamwamuna ndi kapolo wako wamkazi, azipumula monga iwe.+ 15 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo+ ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula.+ N’chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamula kuti uzisunga tsiku la sabata.+

16 “‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ monga mmene Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako atalike, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino+ m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

17 “‘Usaphe munthu.*+

18 “‘Usachite chigololo.+

19 “‘Usabe.+

20 “‘Usapereke umboni wonamizira mnzako.+

21 “‘Usalakelake mkazi wa mnzako.+ Usalakelake mwadyera nyumba ya mnzako, munda wake, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzako.’+

22 “Yehova analankhula Mawu* amenewa mokweza kumpingo wanu wonse, kuchokera pakati pa moto m’phiri,+ pamene kunachita mtambo wakuda ndi mdima wandiweyani, ndipo pa Mawuwo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema n’kundipatsa.+

23 “Ndiyeno mutangomva mawu amenewo kuchokera pamalo amdima, phiri likuyaka moto,+ munabwera kwa ine. Atsogoleri onse a mafuko anu ndi akulu anu onse anabwera kwa ine. 24 Pamenepo munati, ‘Yehova Mulungu wathu watisonyezatu ulemerero wake ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera pakati pa moto.+ Lero taona kuti Mulungu angalankhule ndi munthu, munthuyo n’kukhalabe ndi moyo.+ 25 Moto waukuluwu utipsereza.+ Tiferenji tsono? Tikapitiriza kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wathu tifa basi.+ 26 Pakuti ndani mwa anthu onse amene anamvetserapo mawu a Mulungu wamoyo,+ akulankhula kuchokera pakati pa moto monga mmene tachitira ife n’kukhalabe ndi moyo? 27 Iweyo pita pafupi ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena. Iweyo ndiye udzatiuze zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzakuuza,+ ndipo tidzamvera ndi kuchita zomwezo.’

28 “Motero Yehova anamva mawu anu onse amene munalankhula nane, ndipo Yehova anapitiriza kundiuza kuti, ‘Ndamva mawu amene anthu awa akuuza. Mawu onse amene akuuza ali bwino.+ 29 Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse, kuti iwo ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino mpaka kalekale!*+ 30 Pita ukawauze kuti: “Bwererani kumahema anu.” 31 Koma iwe ima pompano, ndipo ndikuuza malamulo onse, malangizo ndi zigamulo zimene uyenera kuwaphunzitsa+ kuti azikazitsatira m’dziko limene ndikuwapatsa kukhala lawo.’ 32 Ndipo anthu inu muonetsetse kuti mukuchita monga mmene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani.+ Musatembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 33 Muyende m’njira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulani,+ kuti mukhale ndi moyo ndi kuti zinthu zikuyendereni bwino+ ndiponso kuti mutalikitsedi masiku anu m’dziko limene mudzalitenga kukhala lanu.

6 “Tsopano amenewa ndiwo malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu walamula kuti ndikuphunzitseni,+ kuti muzikazitsatira m’dziko limene mukuwolokerako kukalitenga kukhala lanu. 2 Muyenera kuphunzira zimenezi kuti muziopa+ Yehova Mulungu wanu, n’cholinga choti masiku onse a moyo wanu muzisunga mfundo zake ndi malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ ndiponso kuti masiku anu atalike.+ 3 Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira mfundo ndi malamulo ake mosamala,+ kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ ndi kuti muchuluke kwambiri m’dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga mmene Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.+

4 “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.*+ 5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse,+ moyo wako wonse,+ ndi mphamvu zako zonse.+ 6 Ndipo mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako,+ 7 ndi kuwakhomereza mwa ana ako.+ Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona+ ndi podzuka. 8 Uziwamanga padzanja lako+ monga chizindikiro, ndipo azikhala ngati chomanga pamphumi pako,*+ 9 ndiponso uziwalemba pafelemu la khomo la nyumba yako ndi pazipata za mzinda wanu.+

10 “Ndiyeno Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene analumbirira makolo ako Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsa,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yooneka bwino imene sunamange ndiwe,+ 11 yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino zimene sunaikemo ndiwe, ndi zitsime* zimene sunakumbe ndiwe, minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene sunabzale ndiwe, n’kudya ndi kukhuta,+ 12 samala kuti usaiwale+ Yehova amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo. 13 Uziopa Yehova Mulungu wako+ ndi kum’tumikira,+ ndipo uzilumbira pa dzina lake.+ 14 Musatsatire milungu ina, milungu iliyonse ya anthu okuzungulirani,+ 15 (pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi).+ Musatsatire milungu ina kuopera kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu ungakuyakireni,+ ndipo angakufafanizeni padziko lapansi.+

16 “Musamuyese, Yehova Mulungu wanu,+ mmene munamuyesera pa Masa.*+ 17 Muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ maumboni ake+ ndi zigamulo+ zake zimene wakupatsani.+ 18 Ndipo muzichita zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova kuti zikuyendereni bwino,+ ndi kuti mukalowedi m’dziko labwino limene Yehova analumbirira makolo anu,+ ndi kulitenga kukhala lanu, 19 mwa kukankhira adani anu kutali monga mmene Yehova analonjezera.+

20 “Mwana wako akadzakufunsa tsiku lina m’tsogolo+ kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo izi zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani, zimatanthauza chiyani?’ 21 Pamenepo mwana wakoyo udzamuyankhe kuti, ‘Tinakhala akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu.+ 22 Motero Yehova anali kuchita zizindikiro ndi zozizwitsa+ zazikulu ndiponso zodzetsa masoka, mu Iguputo yense, kwa Farao ndi kwa onse a m’nyumba mwake ife tikuona.+ 23 Ndipo anatitulutsa kumeneko kuti atibweretse kuno kudzatipatsa dziko limene analumbirira makolo athu.+ 24 Choncho Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa,+ tiziopa Yehova Mulungu wathu ndi kupindula nthawi zonse,+ kuti tikhale ndi moyo monga mmene zilili lero.+ 25 Ndipo tikatsatira malamulo onsewa monga mmene Yehova Mulungu wathu watilamulira,+ ndiye kuti tikuchita chilungamo+ pamaso pake.’

7 “Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako,+ adzakuchotsera mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotsera Ahiti,+ Agirigasi,+ Aamori,+ Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi+ ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iwe.+ 2 Yehova Mulungu wako adzawapereka ndithu kwa iwe ndipo udzawagonjetse.+ Udzawawononge ndithu+ ndipo usadzachite nawo pangano kapena kuwakomera mtima.+ 3 Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna.+ 4 Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina.+ Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani ndithu mofulumira.+

5 “Koma inu mudzawachitire zotsatirazi: Mudzagwetse maguwa awo ansembe+ ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzadule+ mizati yawo yopatulika+ ndi kutentha zifaniziro zawo zogoba.+ 6 Pakuti ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.+ Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, mwa anthu onse okhala padziko lapansi.+

7 “Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse,+ chifukwatu mtundu wanu unali waung’ono mwa mitundu yonse.+ 8 Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu+ kuti akulanditseni m’nyumba yaukapolo,+ m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani,+ komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+ 9 Ndipo iwe ukudziwa bwino kuti Yehova Mulungu wako ndi Mulungu woona,+ Mulungu wokhulupirika,+ wosunga pangano+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake ku mibadwo masauzande,+ 10 koma wobwezera munthu wodana ndi Mulunguyo mwa kumuwononga+ pamasom’pamaso. Sadzazengereza kuwononga munthu amene amadana ndi Mulungu. Adzam’bwezera pamasom’pamaso. 11 Uzisunga malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene ndikukupatsa lero, mwa kuzitsatira.+

12 “Ndiyeno mukapitiriza kumvera zigamulo zimenezi ndi kuzisunga,+ Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano+ ndi kukusonyezani kukoma mtima kosatha, zimene analumbirira makolo anu.+ 13 Ndipo adzakukondani ndithu, kukudalitsani,+ kukuchulukitsani+ ndi kudalitsa zipatso za mimba yanu+ ndi zipatso za nthaka yanu.+ Adzadalitsa mbewu zanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta anu, ana a ng’ombe zanu ndi ana a nkhosa zanu,+ m’dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.+ 14 Inu mudzakhala odalitsika mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+ 15 Yehova adzakuchotserani matenda onse. Ndipo sadzakugwetserani matenda onse oipa a ku Iguputo amene inu mukuwadziwa,+ koma adzawagwetsera pa onse odana nanu. 16 Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+

17 “Ukaganiza mumtima mwako kuti, ‘Mitundu iyi yandikulira kwambiri. Ndingathe bwanji kuipitikitsa?’+ 18 Usaiope.+ Nthawi zonse uzikumbukira zimene Yehova Mulungu wako anachitira Farao ndi Iguputo yense.+ 19 Uzikumbukira mayesero aakulu amene maso ako anaona,+ zizindikiro, zozizwitsa+ ndiponso dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula+ umene Yehova Mulungu wako anakutulutsa nawo m’dzikolo.+ Umu ndi mmene Yehova Mulungu wako adzachitira ndi anthu a mitundu yonse amene ukuwaopa.+ 20 Yehova Mulungu wako adzachititsanso mantha mitima yawo+ kufikira onse otsala+ ndiponso amene anali kubisala pamaso pako atawonongedwa. 21 Usachite nawo mantha pakuti Yehova Mulungu wako, Mulungu wamphamvu ndi wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+

22 “Yehova Mulungu wako adzakankhira mitundu imeneyi kutali ndi iwe, kuichotsa pamaso pako pang’onopang’ono.+ Sadzakulola kuifafaniza mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingakuchulukire ndi kukuwononga. 23 Yehova Mulungu wako adzawaperekadi kwa iwe ndi kuwabalalitsa atasokonezeka kwambiri, kufikira atawonongedwa.+ 24 Adzapereka mafumu awo m’manja mwako,+ ndipo iwe udzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzaima kutsutsana ndi iwe+ kufikira utawafafaniza.+ 25 Mudzatenthe zifaniziro zogoba za milungu yawo.+ Usadzalakelake siliva ndi golide wawo+ kapena kudzitengera zinthu zimenezi,+ kuopera kuti zingakutchere msampha,+ chifukwa zimenezi ndi zonyansa+ kwa Yehova Mulungu wako. 26 Usabweretse m’nyumba mwako zinthu zonyansa kuti iwenso ungawonongedwe mofanana ndi zinthuzo. Uzinyansidwa nazo kwambiri ndi kuipidwa nazo+ chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.+

8 “Muonetsetse kuti mukusunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndi kuti muchulukanedi, n’kupita kukatenga dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.+ 2 Muzikumbukira njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani m’chipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa,+ kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mukanasunga malamulo ake kapena ayi. 3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokukhalitsani ndi njala+ ndi kukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sanawadziwe. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse ochokera m’kamwa mwa Yehova.+ 4 Zovala zanu sizinathe ndipo mapazi anu sanatupe m’zaka 40 zimenezi.+ 5 Inu mukudziwa bwino mumtima mwanu kuti Yehova Mulungu wanu anali kukuwongolerani, ngati mmene bambo amawongolerera mwana wake.+

6 “Muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu mwa kuyenda m’njira zake+ ndi kumuopa.+ 7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani m’dziko labwino,+ dziko la zigwa* za madzi,+ akasupe ndi madzi ochuluka otuluka m’zigwa ndi m’madera a mapiri, 8 dziko la tirigu, balere, mphesa, nkhuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+ 9 dziko limene mudzadya mkate wosaperewera, limenenso simudzasowa kalikonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso m’mapiri ake mudzakumbamo mkuwa.

10 “Mukadzadya ndi kukhuta+ mudzatamandenso+ Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+ 11 Samalani kuti musaiwale+ Yehova Mulungu wanu ndi kusasunga malamulo, zigamulo ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero.+ 12 Samalani, kuopera kuti mungadye ndi kukhuta, kumanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,+ 13 ng’ombe zanu ndi nkhosa zanu n’kuchuluka, siliva ndi golide wanu n’kuwonjezeka ndiponso zinthu zanu zonse n’kukuchulukirani, 14 mtima wanu n’kuyamba kudzikweza+ ndi kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 15 Mungaiwale amene anakuyendetsani m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni,+ zinkhanira ndiponso dziko louma lopanda madzi. Amenenso anakutulutsirani madzi pamwala wolimba ngati nsangalabwi.+ 16 Mungaiwale amene anakudyetsani mana+ m’chipululu, chakudya chimene makolo anu sanachidziwe, pofuna kukuphunzitsani kudzichepetsa+ ndi kuti akuyeseni kuti potsirizira pake akuchitireni zabwino.+ 17 Samalani kuti munganene mumtima mwanu kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza ndi mphamvu zanga ndi nyonga za dzanja langa.’+ 18 Muzikumbukira Yehova Mulungu wanu, chifukwa ndiye amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbirira makolo anu, monga mmene wachitira lero.+

19 “Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu, n’kutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchitirani umboni lero kuti anthu inu mudzatha.+ 20 Mudzatheratu ngati mitundu imene Yehova akuiwononga pamaso panu, chifukwa simudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.+

9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa m’dziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ 2 yokhalanso ndi anthu amphamvu ndi aatali, ana a Anaki,+ amene inu mukuwadziwa ndipo munamva anthu akunena za iwo kuti, ‘Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?’ 3 Ndipo inu mukudziwa bwino lero kuti Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu+ kuti akutsogolereni. Iye ndi moto wowononga.+ Adzawawononga+ ndipo iye ndi amene adzawagonjetsa inu mukuona. Pamenepo mudzawalande dziko lawo ndi kuwawononga mofulumira monga mmene Yehova wakuuzirani.+

4 “Yehova Mulungu wanu akadzawakankhira kutali ndi inu musadzanene mumtima mwanu kuti, ‘Yehova watilowetsa m’dziko lino kuti tilitenge kukhala lathu, chifukwa cha kulungama kwathu,’+ pamene kwenikweni Yehova akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu chifukwa cha kuipa kwawo.+ 5 Sikuti mukulowa m’dziko ili kukalitenga kukhala lanu chifukwa cha kulungama kwanu+ kapena chifukwa cha kuwongoka mtima kwanu.+ Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo,+ ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+ 6 Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+

7 “Kumbukirani izi: Simuyenera kuiwala mmene munaputira Yehova Mulungu wanu m’chipululu.+ Anthu inu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova kuyambira tsiku limene munatuluka m’dziko la Iguputo mpaka kudzafika malo ano.+ 8 Ngakhale ku Horebe, inu munaputa mkwiyo wa Yehova moti Yehova anakukwiyirani kwambiri mpaka kufika pofuna kukufafanizani.+ 9 Nditakwera m’phiri kukalandira miyala iwiri yosema,+ miyala ya pangano limene Yehova anachita nanu,+ ndinakhala m’phirimo masiku 40, usana ndi usiku,+ (sindinadye mkate kapena kumwa madzi,) 10 ndipo Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene chala cha Mulungu chinalembapo.+ Pamiyala iwiri imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu m’phiri, kuchokera pakati pa moto, tsiku limene munasonkhana kumeneko.+ 11 Ndipo atakwana masiku 40, usana ndi usiku, Yehova anandipatsa miyala iwiriyo, miyala ya pangano.+ 12 Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsika mofulumira m’phiri muno, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa ku Iguputo achita zinthu zowawonongetsa.+ Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuyendamo. Adzipangira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.’+ 13 Yehova anandiuza kuti, ‘Ndawaona anthu awa. Haa! Ndi anthu ouma khosi.+ 14 Ndileke ndiwawononge+ ndi kufafaniza dzina lawo pansi pa thambo,+ ndipo ndikupange mtundu wamphamvu ndi waukulu kwambiri kuposa iwo.’+

15 “Kenako ndinatembenuka ndi kutsika m’phirimo pamene phirilo linali kuyaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali m’manja mwanga.+ 16 Nditayang’ana, ndinaona kuti mwachimwira Yehova Mulungu wanu. Munali mutadzipangira mwana wa ng’ombe wachitsulo chosungunula.+ Munali mutapatuka mofulumira panjira imene Yehova anakulamulani kuyendamo.+ 17 Pamenepo ndinatenga miyala iwiriyo ndi kuiponya pansi mwamphamvu ndi manja anga, ndi kuiswa inu mukuona.+ 18 Zitatero ndinadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova masiku 40, usana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinadye mkate kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita ndi kukhumudwitsa Yehova, mwa kuchita zinthu zoipa pamaso pake.+ 19 Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukulu wa Yehova umene unakuyakirani, mpaka kufika pofuna kukufafanizani.+ Koma Yehova anandimveranso pa nthawi imeneyi.+

20 “Yehova anakwiyiranso kwambiri Aroni, mpaka kufika pofuna kumuwononga.+ Koma ine ndinapembedzeranso Mulungu+ pa nthawi imeneyo kuti asawononge Aroni. 21 Ndipo mwana wa ng’ombeyo,+ amene munachimwa pomupanga, ndinamutenga n’kumutentha ndi moto ndi kumuphwanya, n’kumupera mpaka atakhala wosalala ngati fumbi. Kenako ndinamwaza fumbilo mumtsinje wotuluka m’phirimo.+

22 “Kuwonjezera apo, pa Tabera,+ pa Masa+ ndi pa Kibiroti-hatava+ munaputanso mkwiyo wa Yehova.+ 23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Kwerani ndi kukatenga dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ pamenepo munapandukiranso malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake.+ 24 Mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova+ kuyambira tsiku limene ndinakudziwani.

25 “Chotero ndinadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova masiku 40, usana ndi usiku.+ Ndinadzigwetsa choncho chifukwa Yehova anati akufuna kukufafanizani.+ 26 Pamenepo ndinayamba kupembedzera+ Yehova ndi kunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu, amene ndiwo chuma chanu chapadera,+ anthu amene munawawombola ndi mphamvu yanu, amene munawatulutsa mu Iguputo+ ndi dzanja lamphamvu.+ 27 Kumbukirani atumiki anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ Musaone kuuma mtima kwa anthu awa ndi kuipa kwawo ndiponso tchimo lawo,+ 28 kuopera kuti anthu a m’dziko+ limene munatitulutsamo anganene kuti: “Chifukwa Yehova sanathe kuwalowetsa m’dziko limene anawalonjeza, komanso chifukwa chakuti anali kudana nawo, anawatulutsa kuti akawaphere m’chipululu.”+ 29 Iwo ndi anthu anube, chuma chanu chapadera,+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’+

10 “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Dzisemere miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo udzipangire likasa lamatabwa.+ Ukatero ukwere m’phiri muno kwa ine. 2 Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaswa, ndipo udzaiike m’likasalo.’ 3 Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija.+ Kenako ndinakwera m’phiri, miyala iwiriyo ili m’manja mwanga. 4 Pamenepo analemba pamiyalayo mawu ofanana ndi oyamba aja,+ Mawu Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani m’phiri kuchokera pakati pa moto,+ tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo. 5 Ndiyeno ndinatembenuka, n’kutsika m’phirimo,+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo m’likasa limene ndinapanga kuti izikhala mmenemo, monga mmene Yehova anandilamulira.+

6 “Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka kuchoka ku Beeroti Bene-yaakana+ kupita ku Mosera. Aroni anafera kumalo amenewo, ndipo anamuikanso kumeneko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe m’malo mwa Aroniyo.+ 7 Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko la zigwa* zokhala ndi madzi ndithu.

8 “Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova pom’tumikira,+ ndi kuti lizidalitsa m’dzina lake kufikira lero.+ 9 N’chifukwa chake Levi alibe gawo ndiponso cholowa+ monga abale ake. Yehova ndiye cholowa chake, monga mmene Yehova Mulungu wanu anamuuzira.+ 10 Ndipo ine ndinakhala m’phirimo masiku ofanana ndi oyamba aja, masiku 40, usana ndi usiku,+ ndipo Yehova anandimveranso pa nthawi imeneyi.+ Yehova sanafune kukuwonongani.+ 11 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsogolera anthu kuti ayambe ulendo, kuti akalowe ndi kutenga dziko limene ndinalumbirira makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+

12 “Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani,+ koposa kuopa+ Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njira zake zonse,+ kukonda+ ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 13 kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake+ zimene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino?+ 14 Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu,+ kumwambamwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi+ ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo. 15 Koma Yehova anadziphatika kwa makolo anu ndi kuwakonda, moti anasankha ana awo obadwa m’mbuyo mwawo,+ inuyo, pakati pa anthu onse monga mmene zilili lero. 16 Mitima yanu muichite mdulidwe+ ndipo musakhalenso ouma khosi.+ 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+ 18 Iye amaperekera chiweruzo ana amasiye* ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo wokhala pakati panu+ moti amam’patsa mkate ndi chofunda. 19 Inunso muzikonda mlendo wokhala pakati panu,+ chifukwa munali alendo m’dziko la Iguputo.+

20 “Muziopa Yehova Mulungu wanu.+ Muzim’tumikira,+ kum’mamatira+ ndi kulumbira pa dzina lake.+ 21 Iye ndi amene muyenera kum’tamanda,+ ndipo iye ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha, zimene mwaziona ndi maso anu.+ 22 Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakuthambo.+

11 “Nthawi zonse uzikonda Yehova Mulungu wako+ ndi kuchita zofuna zake, kutsatira mfundo zake, zigamulo zake+ ndi malamulo ake. 2 Inuyo mukudziwa bwino lero, (sindikulankhulatu ndi ana anu amene sanadziwe ndi kuona chilango* cha Yehova+ Mulungu wanu, ukulu wake+ ndi dzanja lake lamphamvu+ ndi mkono wake wotambasula,+ 3 kapena zizindikiro ndi zochita zake zimene anachita pakati pa dziko la Iguputo+ kwa Farao mfumu ya Iguputo, ndi zimene anachitira dziko lake lonse. 4 Amenenso sanaone zimene Mulungu anachitira gulu lankhondo la Aiguputo, mahatchi* ake ndi magaleta* ake ankhondo, amene anawamiza m’madzi a m’Nyanja Yofiira pamene anali kukuthamangitsani,+ ndipo Yehova anawononga Iguputo moti ndi mmene zilili kufikira lero.+ 5 Sindikulankhula ndi ana anu amene sanaone zimene Mulungu wakuchitirani m’chipululu kudzafika malo ano, 6 kapena zimene anachitira Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni, pamene dziko linatsegula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi mabanja awo, mahema awo, ndi chamoyo china chilichonse chimene chinali pakati pawo. Dziko linawameza ali pakati pa Aisiraeli onse).+ 7 Pakuti inu munaona ndi maso anu zochita zonse zazikulu zimene Yehova anachita.+

8 “Chotero muzisunga malamulo onse+ amene ndikukupatsani lero, kuti mukhale amphamvu ndi kuti mulowedi m’dziko limene mukuwolokerako ndi kulitenga kukhala lanu,+ 9 kutinso mutalikitse masiku anu+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzawapatsa iwowo ndi mbewu yawo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+

10 “Pakuti dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu, si lofanana ndi dziko la Iguputo limene munatulukamo. Kumeneko munali kufesa mbewu zanu ndi kuzithirira ndi mapazi* anu, ngati kuti mukuthirira dimba la ndiwo zamasamba. 11 Koma dziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Ilo limamwa madzi a mvula, madzi ochokera kumwamba. 12 Limenelo ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu akulisamalira. Nthawi zonse maso+ a Yehova Mulungu wanu amakhala padziko limeneli, kuyambira kuchiyambi kwa chaka mpaka kumapeto.

13 “Ndiyeno mukadzamveradi malamulo anga+ amene ndikukupatsani lero, moti n’kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 14 iyenso* adzakupatsani mvula pa nthawi yake m’dziko lanu,+ mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza,+ ndipo mudzakololadi mbewu zanu ndi kukhaladi ndi vinyo wotsekemera* komanso mafuta. 15 Adzameretsanso msipu m’dziko lanu kuti ziweto zanu zidye,+ ndipo inu mudzadya ndi kukhuta.+ 16 Samalani kuti mitima yanu isakopeke+ ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiweramira.+ 17 Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani. Adzatseka kumwamba moti mvula sidzagwa+ ndipo nthaka sidzatulutsa zipatso zake. Pamenepo mudzafafanizika mwamsanga m’dziko labwinolo limene Yehova akukupatsani.+

18 “Chotero mawu angawa muwasunge m’mitima yanu+ ndi kuwatsatira m’moyo wanu. Muwamange monga chizindikiro padzanja lanu, ndipo akhale ngati chomanga pamphumi panu.*+ 19 Ana anu muwaphunzitsenso mawu amenewa, ndipo muzilankhula nawo za mawuwa mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.+ 20 Muziwalemba pamafelemu a nyumba zanu ndi pazipata za mzinda wanu,+ 21 kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzawapatsa,+ kuti masikuwo achuluke monga masiku a thambo lokhala pamwamba pa dziko.+

22 “Mukasungadi malamulo onsewa+ amene ndikukupatsani, kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda m’njira zake zonse+ ndi kum’mamatira,+ 23 Yehova adzachotsa mitundu yonseyi chifukwa cha inu,+ ndipo mitundu yamphamvu ndi yaikulu kuposa inu mudzailanda dziko.+ 24 Malo alionse amene mapazi anu adzapondapo adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja ya kumadzulo.+ 25 Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani.

26 “Onani, ndikukuikirani pamaso panu lero dalitso ndi temberero:+ 27 dalitsoli mudzalilandira malinga ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ omwe ndikukupatsani lero, 28 ndipo mudzalandira temberero+ limeneli ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ n’kupatuka panjira imene ndikukulamulani lero kuti muziyendamo, n’kuyamba kutsatira milungu ina imene simukuidziwa.

29 “Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani m’dziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu,+ mukatchule dalitsoli paphiri la Gerizimu+ ndipo temberero mukalitchulire paphiri la Ebala.+ 30 Si paja mapiri amenewa ali kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano, m’dziko la Akanani okhala mu Araba,+ moyang’anizana ndi Giligala,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More?+ 31 Pakuti mukuwoloka Yorodano ndi kukalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala lanu. Mukalitengedi ndi kukhala momwemo.+ 32 Chotero muzisunga mosamala malangizo onse ndi zigamulo zonse+ zimene ndikuika pamaso panu lero.+

12 “Awa ndi malangizo+ ndi zigamulo+ zimene muyenera kuzitsatira mosamala,+ masiku onse amene mudzakhala m’dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu adzakulolani kuti mulitenge kukhala lanu.+ 2 Mudzawononge+ malo onse amene ali pamapiri ataliatali, pazitunda ndi pansi pa mitengo ikuluikulu ya masamba obiriwira, pamene mitundu imene mukukailanda dziko lawo imatumikirirapo milungu yawo.+ 3 Mudzagwetse maguwa awo ansembe+ ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzatenthe mizati yawo yopatulika+ ndi kudula zifaniziro zogoba+ za milungu yawo, ndipo mudzafafanize mayina awo pamalo amenewo.+

4 “Musapembedze Yehova Mulungu wanu m’njira imeneyi,+ 5 koma mudzafunefune malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu onse kuti aikepo dzina lake, kuti lizikhala pamenepo. Amenewo ndiwo malo amene muzidzapitako.+ 6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo. 7 Kumalo amenewo, inuyo ndi mabanja anu muzidzadya zimenezi ndi kusangalala ndi zochita zanu zonse+ pamaso pa Yehova,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.

8 “Musakachite zimene tikuchita kuno lero, aliyense kumangochita zimene akufuna,+ 9 chifukwa simunafike kumalo anu a mpumulo+ ndi kulandira cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 10 Choncho muwoloke Yorodano+ ndi kukhala m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala lanu.+ Iye adzakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, ndipo mudzakhaladi otetezeka.+ 11 Ndiyeno malo+ amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuti pakhale dzina lake n’kumene muzidzabweretsa zonse zimene ndikukulamulani, nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka+ chochokera m’manja mwanu ndi zonse zimene mwasankha kukhala nsembe zanu za lonjezo,+ zimene mudzalonjeza Yehova. 12 Ndipo muzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu, chifukwa iye alibe gawo kapena cholowa monga inu.+ 13 Samalani kuti musadzapereke nsembe zanu zopsereza pamalo ena alionse amene mungaone.+ 14 Koma muzidzapereka nsembe zanu zopsereza pamalo amene Yehova adzasankhe mu limodzi la mafuko anu, ndipo muzichita zonse zimene ndakulamulani pamalo amenewo.+

15 “Muzipha chiweto chanu ndi kudya nyama yake nthawi iliyonse imene mwafuna.+ Muzidya nyamayo malinga ndi dalitso limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani m’mizinda yanu yonse. Munthu wodetsedwa+ komanso munthu woyera ali ndi ufulu wakudya nyamayo, monga mmene amadyera insa ndi mbawala yamphongo.+ 16 Koma musadye magazi ake.+ Muziwathira panthaka ngati madzi.+ 17 Simudzaloledwa kudyera m’mizinda yanu chakhumi cha mbewu zanu,+ vinyo wanu watsopano, mafuta anu, ana oyamba kubadwa a ng’ombe zanu ndi a nkhosa zanu,+ iliyonse mwa nsembe zanu za lonjezo zimene mudzalonjeza, nsembe zanu zaufulu+ kapena chopereka chochokera m’manja mwanu.+ 18 Koma udzazidyera pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Udzazidyera pamalowo iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu. Ndipo uzidzasangalala+ pamaso pa Yehova Mulungu wako pa zochita zako zonse. 19 Samala kuti usataye Mlevi+ masiku onse amene udzakhala m’dzikolo.

20 “Yehova Mulungu wako akadzafutukula malire a dziko lako+ monga mmene wakulonjezera,+ ndipo iwe n’kudzanena kuti, ‘Ndikufuna kudya nyama,’ chifukwa walakalaka kudya nyama, nthawi iliyonse imene mtima wako walakalaka kudya nyama uzidzadya.+ 21 Ndiyeno malo amene Yehova Mulungu wako adzasankha kuikapo dzina lake+ akadzakhala kutali kwambiri ndi iwe, uzidzapha zina mwa ng’ombe zako kapena zina mwa nkhosa zako zimene Yehova wakupatsa, monga mmene ndakulamulira, ndipo uzidzadyera mumzinda mwako nyamazo, nthawi iliyonse imene mtima wako wafuna.+ 22 Uzidzaidya mmene ungadyere insa ndi mbawala yamphongo.+ Munthu wodetsedwa+ komanso munthu woyera ali ndi ufulu wakudya nyamayo. 23 Koma ungokhala wotsimikiza mtima kwambiri kusadya magazi,+ chifukwa magazi ndiwo moyo,+ ndipo suyenera kudya nyama pamodzi ndi moyo wake. 24 Usadye magazi. Uziwathira pansi ngati madzi.+ 25 Usadye magazi, kuti zinthu zikuyendere bwino iweyo+ ndi ana ako obwera m’mbuyo mwako, chifukwa ukatero udzachita choyenera pamaso pa Yehova.+ 26 Pobwera kumalo amene Yehova adzasankhe,+ uzingotenga zinthu zako zopatulika+ zokapereka nsembe, ndi nsembe zako za lonjezo.+ 27 Ukatero uzipereka nsembe zako zopsereza,+ nyama ndi magazi,+ paguwa lansembe la Yehova Mulungu wako. Magazi a nsembe zako uziwathira pansi pafupi ndi guwa lansembe la Yehova+ Mulungu wako, koma nyamayo utha kuidya.

28 “Samala. Uzimvera mawu onsewa amene ndikukuuza,+ kuti zinthu zikuyendere bwino+ mpaka kalekale, iweyo ndi ana ako aamuna obwera m’mbuyo mwako, chifukwa ukatero udzachita chabwino ndi choyenera pamaso pa Yehova Mulungu wako.+

29 “Yehova Mulungu wako akadzawononga ndi kuchotsa pamaso pako mitundu imene ukupita kukailanda dziko,+ ukailandedi dziko lawolo ndi kukhalamo.+ 30 Samala kuti usagwidwe mumsampha wawo,+ pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso pako, kutinso usafufuze za milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inali kutumikira bwanji milungu yawo? Ndithudi inenso ndidzachita zomwezo.’ 31 Usapembedze Yehova Mulungu wako m’njira imeneyi,+ pakuti iwo amachitira milungu yawo zonse zimene zili zonyansa kwa Yehova, zimene iye amadana nazo. Pakuti iwo nthawi zonse amatentha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto monga nsembe kwa milungu yawo.+ 32 Muzichita mosamala mawu onse amene ndikukuuzani.+ Musawonjezepo kapena kuchotsapo kalikonse.+

13 “Mneneri+ kapena wolota maloto+ akauka pakati panu n’kukupatsani chizindikiro kapena chodabwitsa cholosera zam’tsogolo,+ 2 ndipo chizindikiro kapena chodabwitsa chimenecho chachitikadi,+ chimene anachita ponena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina imene simunaidziwe, ndipo tiitumikire,’ 3 musamvere mawu a mneneriyo kapena wolotayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mukukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.+ 4 Muzitsatira Yehova Mulungu wanu, muzimuopa, muzisunga malamulo ake, muzimvera mawu ake, muzim’tumikira ndi kum’mamatira.+ 5 Ndipo mneneri+ kapena wolota malotoyo muzimupha,+ chifukwa walankhula mopandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi kukuwombolani m’nyumba yaukapolo. Munthu ameneyo walankhula zimenezo kuti akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuyendamo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+

6 “M’bale wako, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi ako, kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, mkazi wako wokondedwa kapena bwenzi lako lapamtima,+ akayesa kukupatutsa mwamseri pokuuza kuti, ‘Tiye tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene iwe kapena makolo ako sanaidziwe, 7 milungu ina mwa milungu ya anthu okuzungulirani, okhala pafupi nanu kapena okhala kutali, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena, 8 usavomereze zofuna zake kapena kumumvera.+ Diso lako lisamumvere chifundo ndipo usamumvere chisoni+ kapena kum’bisa kuti um’teteze. 9 Koma umuphe ndithu.+ Dzanja lako lizikhala loyamba kum’ponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ 10 Uzim’ponya miyala kuti afe,+ chifukwa anali kufuna kukupatutsa ndi kukuchotsa kwa Yehova Mulungu wako, amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 11 Pamenepo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachita chinthu choipa chilichonse chofanana ndi chimenechi pakati panu.+

12 “Mu umodzi mwa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti mukhalemo, mukadzamva kuti, 13 ‘Pakati panu papezeka anthu opanda pake+ amene akufuna kupatutsa anthu mumzinda wawo,+ ponena kuti: “Tiyeni tikatumikire milungu ina,” milungu imene inu simunaidziwe,’ 14 muzifunafuna, kufufuza ndi kufunsitsa za nkhani imeneyo.+ Mukapeza kuti ndi zoonadi, choipa chimenechi chachitikadi pakati panu, 15 muzipha ndithu anthu a mumzindawo ndi lupanga.+ Muziwononga+ ndi lupanga mzindawo ndi chilichonse chimene chili mmenemo, kuphatikizapo ziweto zake. 16 Zofunkha zake zonse muzizisonkhanitsa pakati pa bwalo la mzindawo. Pamenepo muzitentha mzindawo+ ndi zofunkha zake zonse monga nsembe yathunthu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Ndipo mzindawo uzikhala bwinja mpaka kalekale.+ Usadzamangidwenso. 17 Ndipo kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa* kasamamatire kudzanja lanu,+ kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova usiye kukuyakirani+ ndipo akuchitireni chifundo ndi kukumverani chisoni,+ kutinso akuchulukitseni, monga mmene analumbirira makolo anu.+ 18 Motero muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mwa kusunga malamulo ake+ onse amene ndikukupatsani lero, kuti muzichita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+

14 “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu.+ Musamadzichekecheke+ kapena kumeta+ nsidze* zanu chifukwa cha anthu akufa. 2 Pakuti ndinu anthu oyera+ kwa Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova wakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera,+ mwa anthu onse okhala padziko lapansi.

3 “Musadye chinthu chilichonse chonyansa.+ 4 Mitundu ya nyama zimene muyenera kudya ndi izi:+ ng’ombe, nkhosa, mbuzi, 5 mbawala yamphongo, insa, ngondo,+ mbuzi yakuthengo, mphalapala, nkhosa yakuthengo ndi chinkhoma. 6 Nyama iliyonse ya ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati imenenso imabzikula,+ imeneyo mungadye. 7 Simuyenera kudya mitundu iyi yokha mwa nyama zonse zimene zimabzikula kapena zokhala ndi ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati: ngamila,+ kalulu+ ndi mbira,+ chifukwa zimabzikula koma si zogawanika ziboda. Nyama zimenezi n’zodetsedwa kwa inu. 8 Musamadyenso nkhumba+ chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake ndipo ikafa musamaikhudze.+

9 “Mwa mitundu yonse ya zinthu zokhala m’madzi, zimene mungadye ndi izi: Chilichonse chokhala ndi zipsepse ndi mamba mungadye.+ 10 Chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba musadye.+ Chimenecho n’chodetsedwa kwa inu.

11 “Mbalame iliyonse yosadetsedwa mungadye. 12 Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13 mphamba wofiira, mphamba wakuda+ ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14 Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala.+ 15 Musadyenso nthiwatiwa,+ kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi. 16 Musadyenso nkhwezule, mantchichi,+ tsekwe, 17 vuwo,+ muimba, chiswankhono, 18 dokowe, sadzu, mleme+ ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri n’todetsedwa kwa inu.+ Timeneti simuyenera kudya. 20 Cholengedwa chilichonse chouluka chosadetsedwa mungadye.

21 “Musadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Muziipereka kwa mlendo wokhala mumzinda wanu kuti adye, kapena muziigulitsa kwa mlendo* chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.

“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

22 “Usalephere kupereka chakhumi cha mbewu zako zonse zokolola m’munda mwako chaka ndi chaka.+ 23 Uzidzadya zinthu zako pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake. Uzidzadya chakhumi cha mbewu zako,+ kumwa vinyo wako watsopano, kudya mafuta ako, ana oyamba a ng’ombe ndi a nkhosa zako.+ Uzichita zimenezi kuti uphunzire kuopa Yehova Mulungu wako nthawi zonse.+

24 “Ndiyeno ulendo ukakhala wautali kwa iwe,+ ndipo sungathe kunyamula chakhumicho, popeza malo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuikapo dzina lake+ ali kutali ndi iwe (chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa,)+ 25 uzidzagulitsa chakhumicho ndipo uzidzatenga ndalamazo ndi kuzifumbata m’manja mwako popita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe. 26 Ndalamazo udzagulire chilichonse chimene mtima wako wakhumba,+ kaya ndi ng’ombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa+ ndi chilichonse chimene mtima wako wafuna. Ndipo uzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kukondwera,+ iweyo ndi banja lako. 27 Mlevi wokhala mumzinda wanu usamutaye,+ pakuti alibe gawo kapena cholowa monga iwe.+

28 “Kumapeto kwa zaka zitatu uzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zako zonse m’chaka chimenecho,+ ndipo uzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu. 29 Ndiyeno Mlevi,+ popeza alibe gawo kapena cholowa monga iwe, komanso mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye+ wokhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta kuti Yehova Mulungu wako akudalitse+ pa chilichonse+ chimene dzanja lako likuchita.

15 “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse uzilengeza kuti anthu amene anakongola zinthu zako amasuka ku ngongoleyo. 2 Kumasula anthu angongoleko kuzichitika motere:+ munthu aliyense asafunse ngongole imene anabwereketsa mnzake. Asakakamize mnzake kapena m’bale wake kupereka ngongoleyo,+ chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chiyenera kuperekedwa pamaso pa Yehova.+ 3 Mlendo+ ungam’kakamize kubweza ngongole, koma ngati m’bale wako wakongola chinthu chako chilichonse usam’kakamize kuchibweza. 4 Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu+ m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako.+ 5 Adzakudalitsa ngati udzamveradi mawu a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiradi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lero.+ 6 Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezera ndipo mitundu yambiri idzakongola+ zinthu zako mwa kukupatsa chikole, pamene iwe sudzakongola kanthu. Udzalamulira mitundu yambiri koma mitundu sidzakulamulira.+

7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+ 8 Uzim’kongoza m’bale wako mowolowa manja,+ mulimonse mmene iye wafunira atakupatsa chikole, ndipo uzim’kongoza zimene akusowa. 9 Samala kuti usalankhule mawu achabe mumtima mwako+ kuti, ‘Chaka cha 7, chaka choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ kuti usaolowere manja m’bale wako wosaukayo,+ osam’patsa kalikonse. Pamenepo iye adzafuulira Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira+ ndipo udzapezeka kuti wachimwa.+ 10 Mulimonse mmene zingakhalire uzim’patsa zimene akufunazo,+ ndipo mtima wako usakhale woumira pomupatsa zinthu zimenezo, chifukwa ukakhala wowolowa manja, Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa chilichonse chimene ukuchita ndi pa ntchito zako zonse.+ 11 Pakuti sipadzalephera kukhala wosauka m’dziko lako.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Uzikhala wowolowa manja kwa m’bale wako wovutika ndi wosauka m’dziko lanu.’+

12 “Ngati anakugulitsa m’bale wako, Mheberi wamwamuna kapena wamkazi,+ ndipo wakutumikira zaka 6, m’chaka cha 7 uzim’masula ndi kumulola kuchoka.+ 13 Ndipo ukam’masula ndi kumulola kuchoka, usamulole kuchoka chimanjamanja.+ 14 Uzim’patsako ndithu zina mwa nkhosa zako, mbewu zochokera pamalo ako opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa. Uzim’patsa malinga ndi mmene Yehova Mulungu wako wakudalitsira.+ 15 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola.+ N’chifukwa chake lero ndikukulamula zinthu zimenezi.

16 “Koma kapoloyo akakuuza kuti, ‘Ine sindikusiyani!’ chifukwa chakuti amakukonda komanso amakonda banja lako, popeza unali kukhala naye bwino,+ 17 uzitenga choboolera ndi kuboola khutu lake ali pakhomo, mpaka chobooleracho chigunde chitseko ndipo azikhala kapolo wako moyo wake wonse.+ Uzichitanso zimenezi ndi kapolo wako wamkazi. 18 Zisakhale zovuta kwa iwe kum’masula kuti achoke,+ chifukwa wakutumikira zaka 6, moti malipiro ake akanafanana ndi malipiro a anthu awiri aganyu,+ ndipo Yehova Mulungu wako wakudalitsa pa chilichonse chimene wachita.+

19 “Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa uzim’patulira Yehova Mulungu wako.+ Usagwiritse ntchito mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe, kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa.+ 20 Chaka ndi chaka iweyo ndi banja lako muzidya mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova adzasankhe.+ 21 Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+ 22 Uzimudyera mumzinda wanu ngati mmene umadyera insa ndi mbawala yamphongo.+ Nayenso munthu wodetsedwa komanso munthu woyera azidya.+ 23 Koma magazi ake okha usadye.+ Uziwathira pansi ngati madzi.+

16 “Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+ 2 Uzipereka nsembe ya pasika kwa Yehova Mulungu wako.+ Uzipereka nkhosa ndi ng’ombe+ pamalo amene Yehova adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 3 Usadye nsembeyo pamodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Masiku 7+ uzidya mkate wopanda chofufumitsa, umene ndi mkate wa nsautso, chifukwa unatuluka mofulumira m’dziko la Iguputo.+ Uzichita zimenezi kuti uzikumbukira tsiku limene unatuluka m’dziko la Iguputo, masiku onse a moyo wako.+ 4 Usapezeke ndi mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa m’dziko lako lonse masiku 7.+ Nyama iliyonse imene wapereka nsembe madzulo, pa tsiku loyamba, isagone mpaka m’mawa.+ 5 Sudzaloledwa kupereka nsembe ya pasika mumzinda wanu uliwonse umene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 6 Koma uzipereka nsembe ya pasikayo pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuikapo dzina lake.+ Uzipereka nsembeyo madzulo, dzuwa likangolowa,+ pa nthawi yofanana ndi imene unatuluka mu Iguputo. 7 Uziiwotcha ndi kuidya+ pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe,+ ndipo m’mawa mwake uzitembenuka ndi kubwerera kumahema ako. 8 Kwa masiku 6, uzidya mkate wopanda chofufumitsa, ndipo pa tsiku la 7 uzichitira Yehova Mulungu wako+ msonkhano wapadera. Pa tsikuli usagwire ntchito.

9 “Uziwerenga masabata 7. Uziyamba kuwerenga masabata 7 amenewo kuchokera pamene wayamba kumweta tirigu.+ 10 Ndiyeno uzichitira Yehova Mulungu wako+ chikondwerero cha masabata, popereka nsembe zaufulu zimene ungathe, monga mmene Yehova Mulungu wako angakudalitsire.+ 11 Pamenepo uzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi wokhala mumzinda wanu, mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye*+ ndi mkazi wamasiye,+ amene ali pakati panu. Muzisangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 12 Uzikumbukira kuti unali kapolo ku Iguputo,+ ndipo uzisunga ndi kutsatira malamulo amenewa.+

13 “Uzichita chikondwerero cha misasa+ masiku 7, potuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa. 14 Ndipo uzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. 15 Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa+ pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.+

16 “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.+ Azikaonekera pa chikondwerero cha mkate wopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata+ ndi pa chikondwerero cha misasa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa Yehova chimanjamanja.+ 17 Mphatso yochokera m’manja mwa aliyense izikhala yolingana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

18 “Mudziikire oweruza+ ndi atsogoleri+ m’mizinda yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, malinga ndi mafuko anu. Oweruza ndi atsogoleriwo aziweruza anthu ndi chiweruzo cholungama. 19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama. 20 Uzitsatira chilungamo.+ Ndithudi uzitsatira chilungamo kuti ukhale ndi moyo ndi kukatengadi dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+

21 “Usabzale mtengo wa mtundu uliwonse kuti ukhale mzati woti uziulambira pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wako limene udzadzipangira.+

22 “Ndipo usadziimikire chipilala chopatulika,+ chinthu chimene Yehova Mulungu wako amadana nacho kwambiri.+

17 “Usapereke kwa Yehova Mulungu wako nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+

2 “Pakati panu pakapezeka mwamuna kapena mkazi wochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, mu umodzi mwa mizinda yanu imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo akuphwanya pangano la Mulungu,+ 3 moti akupita kukalambira milungu ina ndi kuigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ chinthu chimene ine sindinakulamuleni,+ 4 ndipo inu mwamva mutauzidwa, ndiponso mutafufuza mwatsimikizira kuti ndi zoona,+ chinthu choipachi chachitikadi mu Isiraeli, 5 muzitulutsira mwamuna kapena mkazi wochita chinthu choipayo kunja kwa mzinda, ndipo muzim’ponya miyala kuti afe.+ 6 Munthuyo aziphedwa mutamva umboni wa pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ Asaphedwe chifukwa cha umboni wa munthu mmodzi.+ 7 Dzanja la mbonizo lizikhala loyamba kum’ponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+

8 “Mlandu wofuna chigamulo ukakukulira kwambiri,+ monga mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma,+ mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano+ umene wachitika mumzinda wanu, pamenepo uzinyamuka ndi kupita kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ 9 Uzipita kwa ansembe+ achilevi ndi kwa woweruza+ amene aziweruza m’masiku amenewo. Uziwafotokozera nkhaniyo ndipo iwo azikuuza chigamulo.+ 10 Zimene akuuza kumalo amene Yehova adzasankhe uzichita zomwezo. Uzionetsetsa kuti ukuchita zonse zimene akulangiza. 11 Uzichita mogwirizana ndi chilamulo chimene akupatsa ndi chigamulo chimene akuuza.+ Usapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa mawu amene akupatsa.+ 12 Munthu amene adzadzikuza mwa kusamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wako kapena mwa kusamvera woweruza,+ munthu ameneyo afe ndithu.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+ 13 Anthu onse adzamva zimenezo ndi kuchita mantha+ ndipo sadzadzikuzanso.

14 “Ukakafika m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, n’kulitengadi kukhala lako ndi kukhalamo,+ pamenepo iwe n’kunena kuti, ‘Ndidziikire mfumu ngati mitundu ina yonse yondizungulira,’+ 15 uzidziikira mfumu imene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Mfumu imene udzadziikire idzachokere pakati pa abale ako. Sudzaloledwa kudziikira mlendo amene si m’bale wako kukhala mfumu. 16 Koma asadzichulukitsire mahatchi+ kapena kuchititsa anthu kubwerera ku Iguputo kuti akakhale ndi mahatchi ochuluka+ pakuti Yehova wakuuzani kuti, ‘Musabwererenso kudzera njira iyi.’ 17 Asachulukitsenso akazi kuti mtima wake ungapatuke,+ ndipo asachulukitsenso kwambiri siliva ndi golide wake.+ 18 Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la chilamulo ichi, kuchokera m’buku limene ansembe achilevi amasunga.+

19 “Buku limeneli azikhala nalo nthawi zonse ndipo aziliwerenga masiku onse a moyo wake,+ kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake ndi kusunga mawu onse a chilamulo ichi, kutinso azitsatira malangizo ake.+ 20 Azichita zimenezi kuti mtima wake usadzikweze pamaso pa abale ake,+ komanso kuti asachoke pachilamulo mwa kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Azichita zimenezi kuti iyeyo ndi ana ake atalikitse masiku a ufumu wawo+ mu Isiraeli.

18 “Ansembe achilevi, kapena kuti fuko lonse la Levi,+ asakhale ndi gawo kapena cholowa pakati pa Isiraeli. Iwo azidya nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Azidya cholowa chake.+ 2 Choncho asalandire cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo,+ monga mmene anawauzira.

3 “Ndipo izi ndi zinthu zimene ansembe ayenera kulandira kuchokera kwa anthu. Amene akupereka nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu. 4 Uziperekanso gawo loyamba la mbewu zako, vinyo wako watsopano, mafuta ndi ubweya wa nkhosa wometedwa moyambirira.+ 5 Pakuti iye ndi amene Yehova Mulungu wako wam’sankha pakati pa mafuko anu onse, kuti iye pamodzi ndi ana ake aimirire ndi kutumikira m’dzina la Yehova nthawi zonse.+

6 “Ngati Mlevi watuluka mu umodzi mwa mizinda yonse ya Isiraeli, umene iye anakhalamo kwa kanthawi,+ ndiyeno wabwera pamalo amene Yehova adzasankhe, chifukwa chakuti mtima wake walakalaka kukatumikira pamalopo,+ 7 azitumikiranso m’dzina la Yehova Mulungu wake mofanana ndi abale ake onse Alevi, amene aimirira kumeneko pamaso pa Yehova.+ 8 Ngakhale kuti wapeza chuma atagulitsa katundu wa makolo ake, gawo la chakudya chake lizikhala lofanana ndi ansembe onse.+

9 “Ukakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usakaphunzire kuchita zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu imeneyo akuchita.+ 10 Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ wochita zamatsenga,+ woombeza,*+ wanyanga,+ 11 kapena wolodza* ena,+ aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu,+ wolosera zam’tsogolo+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wako akuwapitikitsa pamaso pako.+ 13 Ukhale wopanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.+

14 “Mitundu imene ukuilanda dziko inali kumvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma iwe, Yehova Mulungu wako sanakulole kuchita zimenezi.+ 15 Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.+ 16 Adzakupatsani mneneri poyankha zonse zimene munapempha Yehova Mulungu wanu ku Horebe, tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Munapempha kuti, ‘Tiloleni tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuopera kuti tingafe.’+ 17 Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Mawu onse amene iwo anena ali bwino.+ 18 Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamula.+ 19 Pamenepo munthu amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule m’dzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.+

20 “‘Koma mneneri amene adzadzikuza mwa kulankhula m’dzina langa mawu amene sindinamulamule kuti alankhule,+ kapena kulankhula m’dzina la milungu ina,+ mneneri ameneyo afe ndithu.+ 21 Mumtima mwako ukanena kuti: “Tidzadziwa bwanji kuti si Yehova amene walankhula mawuwo?”+ 22 Mneneri akalankhula m’dzina la Yehova, koma mawuwo sanachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti si Yehova amene walankhula mawu amenewo.+ Mneneriyo walankhula mawu amenewo mwa iye yekha, modzikuza. Iwe usachite naye mantha.’+

19 “Yehova Mulungu wako akadzawononga mitundu+ ya m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, iwe n’kuwalandadi dzikolo ndi kukhala m’mizinda yawo ndi m’nyumba zawo,+ 2 udzadzipatulire mizinda itatu pakati pa dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale lako.+ 3 Udzadzilambulire njira yopita kumizindayo ndipo udzagawe dziko limene Yehova Mulungu wako wakupatsa kuti likhale lako. Dzikolo udzaligawe m’zigawo zitatu. Wopha munthu azithawira kumizinda imeneyo.+

4 “Nkhani ya munthu wopha mnzake amene angathawire kumeneko kuti akhale ndi moyo, izikhala yotere: Akapha munthu mosadziwa ndipo sanali kudana naye,+ 5 kapena akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake+ n’kukantha mnzake ndi kumupha, wopha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 6 Akapanda kutero, wobwezera magazi+ angathamangitse wopha munthuyo ndi kum’peza, chifukwa mtunda ndi wautali. Pamenepo angamukanthe ndi kumupha chifukwa chakuti mtima wake ndi wodzaza ndi ukali, ngakhale kuti wopha mnzake mwangoziyo sanayenere kufa+ chifukwa sanali kudana naye. 7 N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Udzipatulire mizinda itatu.’+

8 “Yehova Mulungu wanu akadzafutukula dera lanu malinga ndi zimene analumbirira makolo anu,+ n’kukupatsani dziko lonse limene analonjeza makolo anu kuti adzawapatsa,+ 9 chifukwa chakuti mwasunga malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero mwa kuwatsatira, kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda m’njira zake nthawi zonse,+ pamenepo mudzawonjezere mizinda inanso itatu pa mizinda imeneyi,+ 10 kuti musakhetse magazi a munthu wosalakwa+ pakati pa dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, kotero kuti musakhale ndi mlandu wa magazi.+

11 “Koma pakakhala munthu wodana+ ndi mnzake amene wabisalira ndi kuukira mnzakeyo panjira n’kumukantha ndipo wafa,+ iye n’kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu a mumzinda wakwawo azitumiza anthu kukam’tenga kumeneko, ndipo azim’pereka m’manja mwa wobwezera magazi kuti afe ndithu.+ 13 Diso lako lisamumvere chisoni+ ndipo uzichotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa mu Isiraeli+ kuti zinthu zikuyendere bwino.

14 “Usasunthe zizindikiro za malire a mnzako,+ makolo anu ataika kale malire a cholowa chimene udzalandira, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako.

15 “Munthu akachita tchimo, mboni imodzi si yokwanira kutsimikizira kuti wachitadi cholakwacho kapena tchimo lililonse.+ Muzitsimikizira nkhaniyo mutamva umboni wapakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 16 Munthu akakonzera mnzake chiwembu mwa kupereka umboni wonama wakuti waphwanya lamulo,+ 17 anthu awiri otsutsanawo aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza amene aziweruza masiku amenewo.+ 18 Pamenepo oweruza azifufuza nkhaniyo mosamala.+ Mboniyo ikapezeka kuti ndi yonama ndipo yaneneza m’bale wake mlandu wonama, 19 muziichitira zimene inafuna kuti zichitikire m’bale wakezo,+ ndipo muzichotsa woipayo pakati panu.+ 20 Chotero ena onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 21 Diso lako lisamumvere chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.+

20 “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+ 2 Mukayandikira kuti mumenyane nawo, wansembe azifika pafupi nanu ndi kulankhula ndi anthu+ 3 kuti, ‘Mverani Aisiraeli inu. Lero mukuyandikira adani anu kuti mumenyane nawo. Mitima yanu isachite mantha.+ Musaope ndipo musathawe mwamantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,+ 4 chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyenda limodzi nanu kuti akumenyereni nkhondo ndi kukupulumutsani kwa adani anu.’+

5 “Atsogoleri+ nawonso azilankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali amene wamanga nyumba yatsopano koma sanaitsegulire? Achoke ndi kubwerera kunyumba yakeyo, kuopera kuti angafe pankhondo, ndipo munthu wina angatsegulire nyumbayo.+ 6 Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole za m’munda wakewo.+ 7 Kodi pali amene analonjeza mkazi kuti adzamukwatira ndipo sanamutenge? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake,+ kuopera kuti angafe pankhondo ndipo mwamuna wina angatenge mkaziyo.’ 8 Ndiyeno atsogoleri apitirize kulankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali wamantha ndi wosalimba mtima?+ Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuti angachititse mantha mitima ya abale ake ngati mmene wachitira mtima wake.’+ 9 Atsogoleriwo akamaliza kulankhula ndi anthu, azisankha akulu a magulu ankhondo oti akhale patsogolo pa anthuwo.

10 “Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kumzindawo mfundo za mtendere.+ 11 Ndiyeno ngati mzindawo wakupatsani yankho la mtendere ndipo akutsegulirani zipata zake, pamenepo anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo. Iwo azikutumikirani.+ 12 Koma ngati mzindawo sukukhazikitsa mtendere ndi inu,+ ndipo ukuchita nanu nkhondo, moti inuyo mwauzungulira, 13 Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu m’manja mwanu, ndipo zikatero muzipha mwamuna aliyense ndi lupanga.+ 14 Koma musaphe akazi, ana aang’ono,+ ziweto+ ndi chilichonse chopezeka mumzindawo. Muzifunkha+ zinthu zonse za mumzindawo ndipo muzidya zimene mwafunkha kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

15 “Muzichita zimenezi ndi mizinda yonse yakutali kwambiri ndi inu imene siili pakati pa mizinda ya mitundu iyi. 16 Mizinda yokhayi ya anthu awa a mitundu ina imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, ndi imene simuyenera kusiyamo chilichonse chopuma chili chamoyo,+ 17 chifukwa muyenera kuwawononga ndithu. Mukawononge Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ monga mmene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani. 18 Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zawo zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo, kuti mungachimwire Yehova Mulungu wanu.+

19 “Mukazungulira mzinda kwa masiku ambiri mwa kumenyana nawo kuti muulande, musawononge mitengo yake mwa kuisamulira nkhwangwa. Muyenera kudya zipatso za mitengoyo, chotero simuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wa m’munda ndi munthu kuti muwuukire? 20 Mungathe kuwononga mtengo wokhawo umene mukuudziwa kuti subereka zipatso zakudya. Mtengo woterowo mungaudule ndi kumangira mpanda wozungulira+ mzinda wa adani umene ukuchita nanu nkhondo, kufikira mzindawo utagwa.

21 “Ukapeza munthu wakufa pathengo, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako, ndipo amene wapha munthuyo sakudziwika,+ 2 akulu ndi oweruza anu+ azipita kukayeza mtunda kuchokera pamene pali munthu wakufayo kukafika kumizinda yonse yozungulira malo amene munthuyo wapezekapo. 3 Ndipo azipeza mzinda umene uli pafupi ndi malo amene munthu wophedwayo wapezeka. Pamenepo akulu a mzinda wapafupiwo azitenga ng’ombe yaing’ono yaikazi imene sanaigwiritsepo ntchito, imene sinasenzepo goli n’kukoka chilichonse. 4 Pamenepo akulu a mzindawo azitenga ng’ombeyo ndi kutsikira nayo kuchigwa* chokhala ndi madzi ndithu, chigwa chimene sichinalimidwepo kapena kubzalidwa mbewu. Akafika kumeneko aziipha mwa kuithyola khosi.+

5 “Ansembe, ana a Levi, azifika pafupi chifukwa ndi amene Yehova Mulungu wanu wawasankha kuti am’tumikire+ ndi kudalitsa+ m’dzina la Yehova. Iwo ndiwo ayenera kuthetsa mkangano uliwonse wokhudza choipa chilichonse chimene chachitika.+ 6 Ndiyeno akulu onse a mzinda umene uli pafupi ndi munthu wophedwayo azisamba m’manja+ pamwamba pa ng’ombe imene yathyoledwa khosi m’chigwa ija. 7 Pamenepo aziyankha kuti, ‘Manja athu sanakhetse magazi awa, ndiponso maso athu sanaone magaziwa akukhetsedwa.+ 8 Musawerengere anthu anu Aisiraeli mlanduwu, anthu amene munawawombola,+ inu Yehova, ndipo musaike mlandu wa magazi osalakwa+ pakati pa anthu anu Aisiraeli.’ Akatero mlandu wa magaziwo usakhale pa iwo. 9 Ndipo inuyo mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu,+ chifukwa mudzakhala mutachita choyenera pamaso pa Yehova.+

10 “Ukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani ako, ndipo Yehova Mulungu wako wawapereka m’manja mwako,+ iwe n’kuwagwira ndi kuwatenga,+ 11 ndipo pakati pa anthu ogwidwawo waonapo mkazi wamaonekedwe okongola ndipo wakopeka+ naye ndi kum’tenga kuti akhale mkazi wako, 12 pamenepo uzim’tenga ndi kulowa naye m’nyumba yako. Kenako azimeta tsitsi lake+ ndi kusamalira zikhadabo zake. 13 Azisintha chovala chimene anavala pamene anali kugwidwa ndipo akhale m’nyumba mwako ndi kulira maliro a bambo ake ndi a mayi ake kwa mwezi wathunthu.+ Kenako umutenge kukhala mkazi wako. Akhale mkwatibwi wako ndipo ugone naye. 14 Ndiyeno ngati sukusangalala naye uzimulola kuchoka+ ngati iyenso akuvomereza, koma uonetsetse kuti usamugulitse ndi ndalama. Usam’chitire nkhanza+ pambuyo poti wamunyazitsa.

15 “Mwamuna akakhala ndi akazi awiri, wina wokondedwa ndi wina wosakondedwa, ndipo onse awiri, wokondedwa ndi wosakondedwayo, abereka ana aamuna ndi mwamunayo, koma mwana wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa,+ 16 tsiku limene adzagawa zinthu zake monga cholowa kwa ana ake aamuna, sadzaloledwa kutenga mwana wamwamuna wa mkazi wokondedwa uja ngati mwana wake woyamba kubadwa m’malo mwa mwana wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo, amene ndiyedi woyamba kubadwa.+ 17 Pakuti ayenera kuvomereza kuti mwana wamwamuna wa mkazi wake wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa. Azivomereza mwa kum’patsa magawo awiri pa chilichonse chimene ali nacho,+ chifukwa mwanayo ndiye chiyambi cha mphamvu zake zobereka.+ Mwana ameneyo ndiye woyenera kulandira udindo wa mwana woyamba kubadwa.+

18 “Munthu akakhala ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wopanduka,+ amene samvera mawu a bambo ake kapena a mayi ake,+ ndipo amulangiza koma sawamvera,+ 19 bambo ake ndi mayi ake azimugwira ndi kubwera naye kwa akulu, kuchipata cha mzinda umene akukhala,+ 20 ndipo aziuza akulu a mzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamvera ndiponso ndi wopanduka. Iye samvera mawu athu+ ndipo ndi wosusuka+ ndiponso ndi chidakwa.’+ 21 Pamenepo amuna onse a mumzinda wawo azim’ponya miyala ndi kumupha. Muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha kwambiri.+

22 “Pakakhala munthu amene wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe, ndiyeno munthuyo waphedwa,+ ndipo wam’pachika pamtengo,+ 23 mtembo wake usakhale pamtengopo usiku wonse,+ koma uzionetsetsa kuti wamuika m’manda tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Usaipitse nthaka yako imene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.+

22 “Ukaona ng’ombe kapena nkhosa ya m’bale wako ikusochera usaisiye mwadala.+ Uziikusa ndithu ndi kuipititsa kwa m’bale wako.+ 2 Ngati mwiniwake sakhala pafupi ndi iwe ndiponso sukumudziwa, uzitengera chiwetocho kunyumba yako. Uzisunga chiwetocho kufikira mwiniwakeyo atafika kudzachifufuza ndipo uzim’bwezera.+ 3 Uzichitanso chimodzimodzi ndi bulu wa m’bale wako, nsalu yake, kapena chilichonse chimene m’bale wako wataya iwe n’kuchipeza. Suyenera kungozisiya osazitola.

4 “Ukaona bulu wa m’bale wako kapena ng’ombe yake itagwa pamsewu usailekerere. Uzim’thandiza m’bale wako mwa kuidzutsa.+

5 “Mkazi asavale chovala cha mwamuna ndipo mwamuna asavale chovala cha mkazi,+ pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.

6 “Ukapeza chisa cha mbalame mumtengo kapena pansi, muli ana+ kapena mazira, make atafungatira ana kapena mazirawo, usatenge make ndi ana omwe.+ 7 Uonetsetse kuti wapitikitsa make, koma anawo ungathe kuwatenga. Uzichita zimenezi kuti zinthu zikuyendere bwino ndiponso kuti utalikitse masiku a moyo wako.+

8 “Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga*+ la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.

9 “M’munda wako wa mpesa usabzalemo mbewu zamitundu iwiri,+ kuopera kuti ungakakamizike kupereka zokolola zako zonse ndi mphesa zako kumalo opatulika.

10 “Usamange ng’ombe ndi bulu kuti uzilimitse pamodzi.+

11 “Usavale chovala chimene anachiwomba mophatikiza ubweya wa nkhosa ndi ulusi wa thonje.+

12 “Uzimanga mphonje m’makona anayi a chovala chako.+

13 “Mwamuna akatenga mkazi ndi kugona naye koma sakum’kondanso,+ 14 ndipo akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi, mwakuti wamuipitsira mbiri+ yake ponena kuti, ‘Ine ndinatenga mkazi uyu ndi kugona naye, koma sindinapeze umboni uliwonse woti anali namwali.’+ 15 Pamenepo bambo ndi mayi a mtsikanayo azibweretsa umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali kwa akulu a mzinda kuchipata cha mzindawo.+ 16 Bambo a mtsikanayo aziuza akuluwo kuti, ‘Ine ndinapereka mwana wa mkazi kwa mwamuna uyu kuti akhale mkazi wake ndipo akumuda.+ 17 Pano akumuimba mlandu wochita zinthu zonyansa ndi zochititsa manyazi+ kuti: “Ndaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti mwana wanuyu anali namwali.”+ Koma nawu umboni wa unamwali wa mwana wanga.’ Pamenepo azifunyulula chofunda pamaso pa akulu a mzinda. 18 Ndiyeno akulu+ a mzindawo azigwira mwamunayo ndi kum’langa.+ 19 Akatero azimulipiritsa masekeli* 100 asiliva, ndipo azipereka ndalamazo kwa bambo a mtsikanayo chifukwa waipitsa mbiri ya namwali wa mu Isiraeli.+ Mtsikanayo apitirize kukhala mkazi wake ndipo sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake.

20 “Koma zimenezi zikatsimikizika kuti ndi zoona, palibedi umboni wa unamwali wa mtsikanayo,+ 21 azim’bweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna a mumzindawo azim’ponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ mwa kuchita uhule m’nyumba ya bambo ake.+ Motero muzichotsa woipayo pakati panu.+

22 “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake,+ mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi. Mwamuna wogona ndi mkaziyo ndiponso mkaziyo azifera pamodzi.+ Motero uzichotsa oipawo mu Isiraeli.+

23 “Pakakhala namwali wolonjezedwa kukwatiwa,+ ndipo mwamuna wina wam’peza mumzinda ndi kugona naye,+ 24 onsewo muziwabweretsa kuchipata cha mzindawo ndi kuwaponya miyala kuti afe. Mtsikanayo afe chifukwa chakuti sanakuwe mumzindawo ndipo mwamunayo afe chifukwa waipitsa mkazi wa mnzake.+ Motero muzichotsa oipawo pakati panu.+

25 “Koma ngati mwamunayo wapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo ndipo wamugwira ndi kugona naye, mwamunayo afe yekha. 26 Mtsikanayo musam’chite chilichonse. Iye sanachite tchimo loyenera imfa, chifukwa mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukira mnzake ndi kumupha,+ kuchotsa moyo wake. 27 Popeza kuti anam’peza kuthengo, mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo anakuwa, koma panalibe womulanditsa.

28 “Mwamuna akapeza ndi kugwira mtsikana, namwali wosalonjezedwa kukwatiwa, n’kugona naye+ ndipo onsewo agwidwa,+ 29 mwamunayo azipereka masekeli 50 asiliva kwa bambo a mtsikanayo,+ ndipo akhale mkazi wake chifukwa chakuti wamunyazitsa. Sadzaloledwa kumusiya ukwati masiku onse a moyo wake.+

30 “Pasapezeke mwamuna aliyense wotenga mkazi wa bambo ake kuopera kuti angavule bambo akewo.+

23 “Mwamuna wofulidwa+ mwa kuphwanya mavalo+ ake kapena woduka maliseche asalowe mumpingo wa Yehova.

2 “Mwana wapathengo+ asalowe mumpingo wa Yehova. Ana ake asalowe mumpingo wa Yehova kufikira m’badwo wa 10.

3 “Muamoni kapena Mmowabu asalowe mumpingo wa Yehova.+ Ana awo asalowe mumpingo wa Yehova kufikira m’badwo wa 10, ngakhalenso mpaka kalekale. 4 Chifukwa chake n’chakuti, sanakuthandizeni+ ndi mkate ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ ndiponso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+ 5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ 6 Musachite kanthu kowathandiza kupeza mtendere ndi chitukuko masiku onse a moyo wanu, mpaka kalekale.+

7 “Usaipidwe ndi Mwedomu, chifukwa ndi m’bale wako.+

“Usaipidwe ndi Mwiguputo, chifukwa unali mlendo m’dziko lawo.+ 8 Ana awo a m’badwo wachitatu angalowe mumpingo wa Yehova.

9 “Ukamanga msasa kuti umenyane ndi adani ako, uzidzipatula ku choipa chilichonse.+ 10 Pakati panu pakakhala mwamuna amene sali woyera chifukwa cha chodetsa chochitika usiku,+ azipita kunja kwa msasa. Asalowe mumsasamo.+ 11 Madzulo asambe ndipo dzuwa likalowa angathe kulowa mumsasa.+ 12 Muzikhala ndi malo obisika kunja kwa msasa kumene muzipita. 13 Uzikhalanso ndi chokumbira pamodzi ndi zida zako. Ndiyeno podzithandiza kunja kwa msasa, uzikumba dzenje ndi chokumbiracho ndipo ukamaliza kudzithandiza uzitembenuka ndi kufotsera zoipazo.+ 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+

15 “Kapolo akathawira kwa iwe kuchokera kwa mbuye wake, usam’bweze kwa mbuye wakeyo.+ 16 Apitirize kukhala ndi iwe pakati panu, pamalo alionse amene iye angasankhe mu umodzi mwa mizinda yanu,+ kulikonse kumene wakonda. Usamamuzunze.+

17 “Mwana wamkazi aliyense wachiisiraeli asakhale hule wa pakachisi,+ ndiponso mwana wamwamuna aliyense wachiisiraeli asakhale hule wa pakachisi.*+ 18 Usabweretse malipiro+ a hule kapena malipiro a galu*+ m’nyumba ya Yehova Mulungu wako kuti ukwaniritse lonjezo lililonse, chifukwa zonsezo ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako.

19 “M’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja+ pa ndalama, chakudya+ kapena chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja. 20 Mlendo+ ungamulipiritse chiwongoladzanja, koma m’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa zochita zako zonse m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+

21 “Ukapereka lonjezo kwa Yehova+ Mulungu wako usachedwe kulikwaniritsa kuopera kuti ungachimwe,+ chifukwa Yehova Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwaniritse chimene walonjezacho.+ 22 Koma ukapanda kulonjeza, sunachimwe.+ 23 Uzisunga mawu a pakamwa pako+ ndipo uzikwaniritsa lonjezo limene unapereka kwa Yehova Mulungu wako monga nsembe yaufulu. Uzichita zimenezi chifukwa unalonjeza ndi pakamwa pako.+

24 “Ukapita m’munda wa mpesa wa mnzako uzidya mphesa kungoti ukhute pa nthawiyo, koma usaike zina m’chotengera chako.+

25 “Ukalowa m’munda wa tirigu wa mnzako, uzipulula ndi dzanja lako tirigu yekhayo amene wacha, koma usamwete tirigu wa mnzako ndi chikwakwa.+

24 “Mwamuna akatenga mkazi kuti akhale mkazi wake, ndiyeno ngati mkaziyo sanamusangalatse chifukwa wam’peza ndi vuto linalake,+ azimulembera kalata yothetsera ukwati+ ndi kum’patsa m’manja mwake, n’kumuchotsa panyumba pake.+ 2 Pamenepo mkaziyo azituluka m’nyumba ya mwamunayo ndi kukakhala mkazi wa mwamuna wina.+ 3 Mwamuna wachiwiriyu akadana nayenso mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati n’kuiika m’manja mwake ndi kum’chotsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyu amene anam’tenga kukhala mkazi wake wamwalira, 4 mwamuna woyamba amene anam’chotsa uja sadzaloledwa kum’tenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa.+ Kuchita zimenezo n’konyansa pamaso pa Yehova, chotero usachimwitse dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.

5 “Mwamuna akatenga mkazi watsopano,+ sayenera kukhala m’gulu lankhondo, ndiponso asakakamizidwe kuchita china chilichonse. Akhale kunyumba osachita zinthu zimenezi kwa chaka chimodzi kuti asangalatse mkazi amene watenga.+

6 “Munthu asalande mnzake mphero kapena mwala woperera monga chikole.+ Kumulanda zimenezi monga chikole ndiko kumulanda moyo.

7 “Munthu akaba+ mmodzi mwa abale ake, ana a Isiraeli, n’kumuchitira nkhanza ndiponso kum’gulitsa,+ wakuba munthuyo afe ndithu. Muzichotsa woipayo pakati panu.+

8 “Samalani ndi mliri wa khate+ ndi kuonetsetsa kuti mukuchita zonse zimene ansembe achilevi adzakulangizani.+ Muzichita mosamala zonse zimene ndawalamula.+ 9 Muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu panjira mutatuluka m’dziko la Iguputo.+

10 “Ukakongoza mnzako ngongole ya mtundu wina uliwonse,+ usamalowe m’nyumba yake kukatenga chimene walonjeza kukupatsa monga chikole.+ 11 Uziima panja, ndipo munthu amene wam’kongozayo azibweretsa yekha chikolecho kwa iwe, panjapo. 12 Ngati munthuyo ndi wovutika, usagone ndi chinthu chake chimene wakupatsa monga chikolecho.+ 13 Uzionetsetsa kuti wam’bwezera chikolecho dzuwa likangolowa,+ kuti akagone m’chovala chake.+ Pamenepo adzakudalitsa,+ ndipo udzakhala utachita chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wako.+

14 “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu, amene ali m’mizinda yanu.+ 15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+

16 “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.+

17 “Usapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo+ kapena mlandu wa mwana wamasiye,*+ ndipo usalande mkazi wamasiye chovala chake monga chikole.+ 18 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo, ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola kumeneko.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi.

19 “Ukaiwala mtolo wa tirigu pokolola m’munda wako,+ usabwerere kukatenga mtolowo. Uzisiyira mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Uzichita zimenezi kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita.+

20 “Pokolola maolivi mwa kukwapula mitengo yake, usabwerere m’mbuyo kukaona ngati m’nthambi zake muli zipatso zotsala. Zimenezo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+

21 “Pokolola mphesa m’munda wako, usabwerere kukakunkha zotsala. Mphesa zotsalazo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. 22 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi.+

25 “Amuna akakangana+ n’kupita kwa oweruza,+ oweruzawo azigamula mlanduwo. Wolungama azimuweruza kuti ndi wolungama ndipo woipa azimuweruza kuti ndi woipa.+ 2 Ngati woipayo akuyenera kukwapulidwa,+ woweruza azilamula kuti woipayo amugoneke pansi, ndipo azim’kwapula+ pamaso pa woweruzayo. Azimukwapula zikoti zogwirizana ndi choipa chimene wachita. 3 Azimukwapula zikoti 40. Asapitirire pamenepo, kuopera kuti akapitiriza kumukwapula zikoti zambiri+ anganyazitse m’bale wako pamaso pako.

4 “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.+

5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+ 6 Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, atenge dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la m’bale wake lisafafanizike mu Isiraeli.+

7 “Ngati mwamunayo sakufuna kutenga mkazi wamasiye wa m’bale wakeyo, mkaziyo azinyamuka ndi kupita kuchipata kwa akulu+ ndi kuwauza kuti, ‘M’bale wa mwamuna wanga wakana kusunga dzina la m’bale wake mu Isiraeli. Sanavomereze kuchita ukwati wa pachilamu ndi ine.’ 8 Pamenepo akulu a mzindawo amuitane ndi kulankhula naye. Iye aime pamaso pawo ndi kunena kuti, ‘Sindikufuna kutenga mkazi ameneyu.’+ 9 Zikatero mkazi wamasiyeyo aziyandikira m’bale wa mwamuna wakeyo akuluwo akuona ndipo azim’vula nsapato+ ndi kumulavulira kumaso.+ Pamenepo azinena kuti, ‘Izi ndiye zoyenera kuchitikira munthu wokana kumanga nyumba ya m’bale wake.’+ 10 Ndiyeno mu Isiraeli monse azidziwika ndi dzina lakuti, ‘Nyumba ya amene anavulidwa nsapato uja.’

11 “Amuna akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi mwa amunawo wabwera kudzalanditsa mwamuna wake m’manja mwa amene akumumenya, ndipo mkaziyo watambasula dzanja ndi kugwira mwamuna winayo kumaliseche,+ 12 uzidula dzanja la mkaziyo. Diso lako lisamve chisoni.+

13 “M’thumba lako, usakhale ndi miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ usakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waung’ono. 14 Usakhale ndi miyezo iwiri yosiyana ya efa*+ m’nyumba yako, usakhale ndi muyezo waukulu ndi muyezo waung’ono. 15 Muyezo wako woyezera kulemera kwa chinthu uzikhala wolondola ndi woyenera. Muyezo wako wa efa uzikhala wolondola ndi woyenera kuti masiku ako achuluke m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ 16 Pakuti aliyense wochita zimenezi, aliyense wosachita chilungamo, n’ngonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+

17 “Muzikumbukira zimene Aamaleki anakuchitirani panjira pamene munali kutuluka mu Iguputo.+ 18 Iwo anakumana nanu panjira ndi kupha anthu oyenda movutika m’gulu lanu amene anali kumbuyo. Iwo anachita izi pamene munali olefuka ndi otopa ndipo sanaope Mulungu.+ 19 Motero Yehova Mulungu wanu akakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mufafanize dzina la Amaleki pansi pa thambo.+ Musaiwale zimenezi.

26 “Ndiyeno ukakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa chako, n’kulitenga kukhala lako ndi kukhalamo,+ 2 ukatenge zina mwa zipatso zoyambirira+ pa zipatso zonse za m’munda mwako zimene udzakolola m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. Ukaziike m’dengu ndi kupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuika dzina lake.+ 3 Uzikapita kwa wansembe+ amene azidzatumikira masiku amenewo ndi kumuuza kuti, ‘Ndikuvomereza lero pamaso pa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowadi m’dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa.’+

4 “Wansembeyo azikalandira dengulo m’manja mwako ndi kuliika pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wako. 5 Pamenepo uzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Bambo anga anali Msiriya+ wotsala pang’ono kufa. Anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa chabe+ a m’banja lake kukakhala kumeneko monga mlendo, koma anakhaladi mtundu waukulu ndi wamphamvu kumeneko.+ 6 Ndipo Aiguputo anayamba kutichitira zoipa, kutizunza ndi kutigwiritsa ntchito yowawa yaukapolo.+ 7 Pamenepo tinayamba kufuulira Yehova Mulungu wa makolo athu,+ ndipo Yehova anamva mawu athu+ ndi kuona nsautso yathu, mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu.+ 8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula,+ zoopsa zazikulu,+ zizindikiro ndi zozizwitsa.+ 9 Ndiyeno anatibweretsa kumalo ano ndi kutipatsa dziko ili, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za m’dziko limene Yehova anandipatsa.’+

“Pamenepo uzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kugwada pamaso pa Yehova Mulungu wako.+ 11 Uzikasangalala+ chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wako wapatsa iwe ndi nyumba yako, zimene wapatsa iweyo komanso Mlevi ndi mlendo wokhala pakati panu.+

12 “Ukamaliza kusonkhanitsa chakhumi chonse+ cha zokolola zako m’chaka chachitatu,+ chaka chopereka chakhumi, uzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye. Amenewa azidzadya ndi kukhuta chakhumicho m’mizinda yanu.+ 13 Ukatero uzidzanena pamaso pa Yehova Mulungu wako kuti, ‘Ndachotsa chinthu chopatulika m’nyumba mwanga ndi kuchipereka kwa Mlevi, mlendo wokhala pakati pathu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Ndachita zimenezi mogwirizana ndi malamulo onse amene munandipatsa. Sindinaphwanye malamulo anu kapena kuwaiwala.+ 14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nyengo yanga yakulira, kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka gawo lake chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga. Ndachita mogwirizana ndi zonse zimene munandilamula. 15 Yang’anani pansi kuchokera kumwamba, kumalo anu oyera okhalako,+ ndipo mudalitse anthu anu Aisiraeli+ ndi dziko limene mwatipatsa, dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ monga mmene munalumbirira makolo athu.’+

16 “Lero Yehova Mulungu wanu akukulamulani kutsatira malangizo ndi zigamulo+ zimenezi. Motero muzisunga ndi kutsatira zimenezi ndi mtima wanu+ wonse ndi moyo wanu wonse.+ 17 Inu lero mwachititsa Yehova kunena kuti adzakhala Mulungu wanu mukamayenda m’njira zake ndi kusunga malangizo,+ malamulo+ ndi zigamulo zake+ ndiponso kumvera mawu ake.+ 18 Ndipo lero Yehova wakuchititsani kunena kuti mudzakhala anthu ake, chuma chapadera,+ monga mmene anakulonjezerani,+ ndiponso kuti mudzasunga malamulo ake onse, 19 ndi kuti adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga.+ Zimenezi zidzakudzetserani chitamando, mbiri yabwino ndi kukongola, mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu,+ monga mmene anakulonjezerani.”

27 Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli anapitiriza kuuza anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero.+ 2 Mukawoloka Yorodano+ ndi kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muimike miyala ikuluikulu ndi kuipaka utoto woyera. 3 Ndiyeno mukawoloka,+ mulembe pamiyalapo mawu onse a chilamulochi+ kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, malinga ndi zimene Yehova Mulungu wa makolo anu wakuuzani.+ 4 Choncho mukawoloka Yorodano, muimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ monga mmene ndakulamulirani lero, ndipo muipake utoto woyera.+ 5 Mumangirenso Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+ 6 Muzigwiritsa ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo.+ 7 Muzipereka nsembe zachiyanjano+ ndi kuzidyera pamenepo,+ ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ 8 Mulembe mawu onse a chilamulochi pamiyalayo,+ muwalembe moonekera bwino.”+

9 Kenako Mose ndi ansembe achilevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+ 10 Choncho muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake,+ amene ndikukupatsani lero.”

11 Tsiku limenelo Mose anapitiriza kulankhula ndi anthuwo kuti: 12 “Amene adzaimirira ndi kudalitsa anthu paphiri la Gerizimu+ mukawoloka Yorodano ndi awa: Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Amene adzaimirira kuti avomere pamene matemberero+ akutchulidwa paphiri la Ebala+ ndi awa: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali. 14 Pamenepo Alevi azinena mawu awa mokweza kuuza mwamuna aliyense wa Isiraeli+ kuti:

15 “‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndi kuchibisa. Chifanizirocho ndi chinthu chonyansa kwa Yehova,+ Mulungu wopanga manja a mmisiri wa matabwa ndi zitsulo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)*+

16 “‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

17 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

18 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa wakhungu.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

19 “‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza+ chiweruzo+ cha mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

20 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wavula bambo akewo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

21 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona nyama iliyonse.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

22 “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

23 “‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

24 “‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake ndi kumupha.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

25 “‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti akanthe ndi kupheratu munthu, kuti akhetse magazi a munthu wosachimwa.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

26 “‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a m’chilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

28 “Ukamveradi mawu a Yehova Mulungu wako mwa kuonetsetsa kuti ukutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsa lero,+ Yehova Mulungu wako adzakukweza ndithu pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi.+ 2 Madalitso onsewa adzakutsata ndi kukupeza+ chifukwa ukumvera mawu a Yehova Mulungu wako:

3 “Udzakhala wodalitsika mumzinda,+ udzakhala wodalitsika m’munda.+

4 “Chidzadalitsika chipatso cha mimba yako,+ chipatso cha m’dziko lanu, chipatso cha ziweto zako,+ ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.+

5 “Lidzadalitsika dengu lako+ ndi chiwiya chako chokandiramo ufa.+

6 “Udzadalitsika pa zochita zako zonse.+

7 “Yehova adzachititsa adani ako amene adzakuukira kugonja pamaso pako.+ Pobwera kwa iwe adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pako, adzadutsa njira 7.+ 8 Yehova adzaika madalitso pankhokwe+ ndi pa zochita zako zonse+ ndipo adzakudalitsa m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 9 Yehova adzakukhazikitsani monga anthu ake oyera,+ monga mmene analumbirira kwa inu,+ chifukwa mwapitiriza kusunga malamulo+ a Yehova Mulungu wanu ndipo mwayenda m’njira zake. 10 Pamenepo mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+

11 “Yehova adzachulukitsa chuma chako pa zipatso za mimba yako,+ zipatso za ziweto zako ndi zipatso za m’munda mwako,+ m’dziko limene Yehova analumbirira makolo ako kuti adzakupatsa.+ 12 Yehova adzakutsegulira kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatse mvula pa nyengo yake+ m’dziko lako ndi kuti adalitse ntchito iliyonse ya manja ako.+ Udzakongoza mitundu yambiri koma iwe sudzakongola kanthu kwa iwo.+ 13 Yehova adzakuchititsa kukhala kumutu osati kumchira. Pamenepo udzangokhala pamwamba+ ndipo sudzakhala m’munsi, chifukwa ukumvera malamulo+ a Yehova Mulungu wako amene ndikukupatsa lero kuti uwasunge ndi kuwatsatira. 14 Usapatuke pa mawu onse amene ndikukulamula lero, kupita kudzanja lamanja kapena lamanzere+ kuti utsatire milungu ina ndi kuitumikira.+

15 “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kuonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, matemberero otsatirawa adzakugwerani ndi kukupezani:+

16 “Udzakhala wotembereredwa mumzinda,+ udzakhala wotembereredwa m’munda.+

17 “Lidzakhala lotembereredwa dengu lako+ ndi chiwiya chako chokandiramo ufa.+

18 “Chidzakhala chotembereredwa chipatso cha mimba yako,+ chipatso cha nthaka yako,+ ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.+

19 “Udzakhala wotembereredwa pa zochita zako zonse.+

20 “Yehova adzakutumizira matemberero,+ chisokonezo+ ndi chilango+ pa ntchito zako zonse zimene ukuyesa kugwira. Adzakuchitira zimenezi kufikira utafafanizidwa ndi kutha mofulumira, chifukwa cha kuipa kwa zochita zako popeza kuti wandisiya.+ 21 Yehova adzachititsa mliri kukumamatira kufikira atakufafaniza m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+ 22 Yehova adzakulanga ndi chifuwa chachikulu,+ kuphwanya kwa thupi koopsa, kutupa, kutentha thupi kwambiri, lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu+ ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakusautsa kufikira utawonongeka. 23 Thambo limene lili pamwamba pa mutu wako lidzakhala ngati mkuwa, ndipo nthaka yako idzakhala ngati chitsulo.+ 24 Yehova adzakugwetsera mchenga ndi fumbi ngati mvula m’dziko lako. Adzakugwetsera zimenezi kuchokera kumwamba kufikira utafafanizika. 25 Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+ 26 Mitembo yanu idzakhala chakudya cha cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+

27 “Yehova adzakulanga ndi zithupsa za ku Iguputo,+ matenda a mudzi,* ziwengo ndi zotupa, ndipo sudzachira matenda amenewa. 28 Yehova adzakulanga ndi misala,+ khungu+ ndipo adzakuchititsa kudabwa kwambiri.+ 29 Udzafufuzafufuza masana ngati mmene wakhungu amafufuzirafufuzira mu mdima,+ ndipo sudzapambana. Iwe wekha udzakhala wodyeredwa ndi kulandidwa zinthu nthawi zonse, popanda wokupulumutsa.+ 30 Udzalonjeza kukwatira mkazi koma mwamuna wina adzamugwirira.+ Udzamanga nyumba koma sudzakhalamo.+ Udzabzala mitengo ya mpesa koma sudzadya zipatso zake.+ 31 Ng’ombe yako idzaphedwa iwe ukuona, koma nyama yake sudzadyako. Bulu wako adzalandidwa ndi achifwamba iwe ukuona, ndipo sudzamuonanso. Nkhosa yako idzaperekedwa kwa adani ako, koma sipadzakhala wokupulumutsa.+ 32 Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaperekedwa kwa anthu ena+ iwe ukuona ndipo udzawalakalaka nthawi zonse, koma manja ako adzakhala opanda mphamvu.+ 33 Anthu amene sunawadziwe adzadya zipatso za m’dziko lako ndi mbewu zako zonse.+ Motero udzakhala wodyeredwa ndi woponderezedwa nthawi zonse.+ 34 Pamenepo udzasokonezeka mutu chifukwa cha zimene maso ako adzaona.+

35 “Yehova adzakulanga ndi zithupsa zonyeka m’mawondo onse ndi m’ntchafu monse. Matenda amenewa adzayambira kumapazi mpaka paliwombo, ndipo sudzachira.+ 36 Yehova adzakuyendetsa+ pamodzi ndi mfumu+ yako imene udzadziikira, kukupititsa ku mtundu umene iweyo kapena makolo ako simunaudziwe. Kumeneko udzatumikira milungu ina, yamtengo kapena yamwala.+ 37 Pamenepo udzakhala chodabwitsa,+ adzakupekera mwambi+ ndi kukutonza pakati pa mitundu yonse ya anthu amene Yehova adzakupititsako.

38 “Udzapita ndi mbewu zambiri kumunda, koma udzakolola zochepa+ chifukwa dzombe lidzadya mbewuzo.+ 39 Udzalimadi ndi kubzala mitengo ya mpesa, koma sudzakolola mphesa zake ndi kumwa vinyo,+ chifukwa mbozi zidzadya mpesawo.+ 40 Udzakhala ndi mitengo ya maolivi m’dera lako lonse, koma sudzadzola mafuta chifukwa maolivi ako adzayoyoka.+ 41 Udzabereka ana aamuna ndi ana aakazi, koma sadzapitiriza kukhala ako chifukwa adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 42 Mitengo yako yonse ndi zipatso za m’dziko lako zidzakhala za tizilombo ta mapiko tochita mkokomo. 43 Mlendo wokhala pakati panu adzapitirizabe kutukuka kukuposani, koma inuyo mudzapitirizabe kutsika pansi.+ 44 Iye adzakhala wokukongoza koma iweyo sudzatha kumukongoza.+ Iye adzakhala mutu koma iweyo udzakhala mchira.+

45 “Matemberero onsewa+ adzakugwera, kukutsatira ndi kukupeza kufikira utafafanizika,+ chifukwa sunamvere mawu a Yehova Mulungu wako mwa kusunga malamulo ndi mfundo zake zimene anakupatsa.+ 46 Matembererowa adzapitiriza pa iwe ndi ana ako monga chizindikiro ndi cholosera mpaka kalekale,+ 47 chifukwa chakuti sunatumikire Yehova Mulungu wako mokondwera, ndi mtima wosangalala,+ pamene unakhala ndi zochuluka pa chilichonse.+ 48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+

49 “Yehova adzautsa mtundu wakutali, kumalekezero a dziko,+ mtundu umene chilankhulo chake sudzachimva.+ Mtunduwo udzakuukira monga mmene chiwombankhanga chimakhwathulira nyama yake,+ 50 mtundu wa nkhope yoopsa+ umene sudzaikira kumbuyo munthu wachikulire kapena kukondera mnyamata.+ 51 Iwo adzadya chipatso cha ziweto zako ndi zipatso za nthaka yako kufikira utafafanizidwa,+ ndipo sadzakusiyirako mbewu, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ng’ombe yako kapena mwana wa nkhosa yako kufikira atakuwonongeratu.+ 52 Chotero adzakuzungulirani m’mizinda yanu yonse kufikira mipanda yanu yaitali ndi yolimba kwambiri imene muzidzaidalira itagwa m’dziko lanu lonse. Adzakuzungulirani ndithu m’mizinda yanu yonse m’dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 53 Pamenepo udzadya chipatso cha mimba yako, mnofu wa ana ako aamuna ndi ana ako aakazi,+ amene Yehova Mulungu wako wakupatsa, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani ako adzakupanikiza nazo.

54 “Koma mwamuna wolobodoka nkhongono ndi wachisasati* pakati panu, adzayang’ana ndi diso+ loipa m’bale wake, mkazi wake wokondedwa ndi ana ake aamuna amene atsala, 55 kuti asagawireko aliyense wa iwo mnofu uliwonse wa ana ake aamuna amene adzawadya. Adzatero poona kuti alibiretu china chilichonse, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene mdani wanu adzakupanikizani nazo m’mizinda yanu yonse.+ 56 Ndipo mkazi wolobodoka nkhongono ndi wachisasati pakati panu, amene sanayesepo n’komwe kupondetsa phazi lake pansi chifukwa cha kuleredwa mwachisasati ndi kulobodoka nkhongono,+ ameneyu adzayang’ana ndi diso loipa mwamuna wake wokondedwa, mwana wake wamwamuna ndi mwana wake wamkazi. 57 Adzayang’ananso ndi diso loipa zotuluka m’mimba mwake pambuyo pobereka komanso ana ake aamuna amene iye anabereka,+ chifukwa adzawadya mseri pokhala wosowa chilichonse chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene mdani wanu adzakupanikizani nazo m’mizinda yanu.+

58 “Ngati sudzatsatira mosamala mawu onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili,+ kuti uziopa dzina laulemerero+ ndi lochititsa manthali,+ dzina lakuti Yehova,+ amene ndi Mulungu wako, 59 Yehova adzakulitsa kwambiri miliri yako ndi miliri ya ana ako. Miliri imeneyo idzakhala yaikulu kwambiri ndi yokhalitsa,+ ndipo udzagwidwa ndi matenda onyansa ndi okhalitsa.+ 60 Adzakubweretsera matenda onse a ku Iguputo amene unachita nawo mantha, ndipo adzakumamatira.+ 61 Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakubweretsera nthenda iliyonse ndi mliri uliwonse umene sunalembedwe m’buku la chilamulo ili, kufikira utafafanizika. 62 Ngakhale kuti mwachuluka ngati nyenyezi zakumwamba,+ mudzatsala ochepa+ chifukwa chosamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.

63 “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+

64 “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+ 65 Pakati pa mitundu imeneyo sudzakhala mwamtendere,+ ndipo sudzapeza malo oti phazi lako liponde kuti lipumulirepo. Kumeneko, Yehova adzakupatsa mtima wachinthenthe,+ adzachititsa maso ako+ khungu ndipo adzakutayitsa mtima. 66 Pamenepo moyo wako udzakhala pangozi yaikulu koopsa, ndipo udzakhala wamantha usiku ndi usana, moti sudzakhala wotsimikiza za moyo wako.+ 67 M’mawa udzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino akanakhala madzulo!’ ndipo madzulo udzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino ukanakhala m’mawa!’ chifukwa cha mantha amene adzagwira mtima wako, ndiponso chifukwa cha zimene maso ako adzaona.+ 68 Yehova adzakubwezerani ku Iguputo pa zombo kudzera njira imene ndinakuuzani kuti, ‘Simudzaionanso.’+ Kumeneko mudzalakalaka kudzigulitsa kwa adani anu kuti mukhale akapolo aamuna ndi aakazi,+ koma sipadzakhala wokugulani.”

29 Awa ndi mawu a pangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi ana a Isiraeli m’dziko la Mowabu, kuwonjezera pa pangano limene anachita nawo ku Horebe.+

2 Choncho Mose anaitana Aisiraeli onse ndi kuwauza kuti: “Inuyo ndinu amene munaona ndi maso m’dziko la Iguputo zonse zimene Yehova anachitira Farao, atumiki ake onse ndi dziko lake lonse.+ 3 Inuyo munaona mayesero,+ zizindikiro zazikulu+ zija ndi zozizwitsa.+ 4 Koma Yehova sanakupatseni mtima woti muthe kuzindikira, maso oti muthe kuona ndi makutu oti muthe kumva, kufikira lero.+ 5 ‘Pamene ndinali kukutsogolerani kwa zaka 40 m’chipululu,+ zovala zanu sizinathe ndiponso nsapato zanu sizinathe kumapazi anu.+ 6 Simunadye mkate,+ simunamwe vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ 7 Ndiyeno munafika pamalo ano, ndipo Sihoni mfumu ya Hesiboni+ ndi Ogi+ mfumu ya Basana anatuluka kudzamenyana nafe nkhondo, koma tinawagonjetsa.+ 8 Kenako tinatenga dziko lawo ndi kulipereka monga cholowa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase.+ 9 Choncho muzisunga mawu a pangano ili kuti zonse zimene muzichita zizikuyenderani bwino.+

10 “Nonsenu mwaima pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu atsogoleri a mafuko, akulu anu, atsogoleri anu, mwamuna aliyense wa mu Isiraeli,+ 11 ana anu, akazi anu,+ alendo+ okhala mkati mwa msasa wanu, kuyambira wokutolerani nkhuni mpaka wokutungirani madzi,+ 12 kuti muchite pangano+ ndi Yehova Mulungu wanu mwa kulumbira, pangano limene Yehova Mulungu wanu akuchita nanu lero.+ 13 Cholinga chake n’chakuti akukhazikitseni lero monga anthu ake+ ndi kuti akuonetseni kuti ndi Mulungu wanu,+ monga mmene anakulonjezerani ndiponso monga mmene analumbirira makolo anu, Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+

14 “Tsopano sindikuchita pangano ili mwa lumbiro ndi inu nokha ayi,+ 15 koma ndikuchita pangano ili ndi anthu amene aimirira ndi ife pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wanu, komanso ndi awo amene sitili nawo pano lero.+ 16 (Pakuti inu mukudziwa bwino mmene tinali kukhalira m’dziko la Iguputo ndi mmene tinadutsira pakati pa anthu a mitundu ina. Podutsa pakati pa mitundu imeneyo,+ 17 munaona zinthu zawo zonyansa ndi mafano awo onyansa,*+ mafano amtengo ndi amwala, asiliva ndi agolide amene anali nawo.) 18 Cholinga cha pangano limeneli n’chakuti, pakati panu pasapezeke mwamuna, mkazi, banja kapena fuko limene mtima wake ukupatuka kusiyana ndi Yehova Mulungu wathu, ndi kupita kukatumikira milungu ya mitundu inayo,+ kuti pakati panu pasapezeke muzu wotulutsa chomera chakupha ndi chitsamba chowawa.+

19 “Ndiyeno zikachitika kuti wina amene wamva mawu a lumbiro+ ili, walankhula modzitama mumtima mwake kuti, ‘Ndidzakhala ndi mtendere+ ngakhale kuti ndidzayenda motsatira zofuna za mtima wanga,’+ koma ali ndi cholinga chowononga wina aliyense, mofanana ndi kukokolola mtengo wothiriridwa bwino ndi wosathiriridwa womwe, 20 Yehova sadzafuna kukhululukira+ munthu woteroyo, m’malomwake mkwiyo+ ndi ukali+ wa Yehova udzamuyakira,+ ndipo matemberero onse olembedwa m’buku+ ili adzakhala pa iye, motero Yehova adzafafanizadi dzina la munthuyo pansi pa thambo. 21 Choncho Yehova adzam’patula+ pa mafuko onse a Isiraeli kuti amudzetsere tsoka, mogwirizana ndi matemberero onse a pangano lolembedwa m’buku ili la chilamulo.

22 “Pamenepo m’badwo wa m’tsogolo, ana anu amene adzabwera pambuyo panu, ndiponso mlendo amene adzachokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi nthenda zimene Yehova wakantha nazo dzikolo,+ adzanena mawu. 23 Adzanena mawuwo akadzaonanso sulufule, mchere+ ndi kutentha,+ moti m’dzikomo simungabzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, mofanana ndi Sodomu ndi Gomora,+ Adima+ ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga mu ukali ndi mkwiyo wake.+ 24 Mitundu yonse idzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mkwiyo wake wayaka kwambiri chonchi?’ 25 Pamenepo anthu adzanena kuti, ‘N’chifukwa chakuti anataya pangano+ la Yehova Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.+ 26 Ndipo anapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, milungu imene sanaidziwe, imenenso sanaloledwe kuti aziilambira.+ 27 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira dziko limeneli mwa kulibweretsera matemberero onse olembedwa m’buku ili.+ 28 Choncho Yehova anawazula m’dziko lawo atapsa mtima,+ ali ndi ukali ndiponso mkwiyo waukulu n’kuwataya m’dziko lina monga mmene zilili lero.’+

29 “Zinthu zobisika+ ndi za Yehova Mulungu wathu, koma zinthu zoululidwa+ ndi zathu ndi ana athu mpaka kalekale, kuti titsatire mawu onse a chilamulo ichi.+

30 “Ndiyeno zikadzachitika kuti mawu onsewa akwaniritsidwa pa inu, madalitso+ ndi matemberero+ amene ndakuikirani pamaso panu, ndipo mwakumbukira mawu amenewa mumtima mwanu+ muli pakati pa mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsirani,+ 2 moti mwabwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ ndi kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,+ mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu, 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ 4 Anthu a mtundu wanu obalalitsidwawo akadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani ndi kukutengani kumeneko.+ 5 Choncho Yehova Mulungu wanu adzakulowetsanidi m’dziko limene makolo anu analitenga kukhala lawo, ndipo inu mudzalitenga kukhala lanu. Pamenepo, adzakuchitirani zabwino ndi kukuchulukitsani kuposa makolo anu.+ 6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+ 7 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaikadi matemberero onsewa pa adani anu, ndi onse odana ndi inu amene anakuzunzani.+

8 “Koma iwe udzatembenuka ndi kumvera mawu a Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsa lero.+ 9 Ndipo Yehova Mulungu wako adzakuchititsa kukhala ndi zinthu zosefukira pa ntchito iliyonse ya manja ako,+ chipatso cha mimba yako, chipatso cha ziweto zako+ ndi chipatso cha nthaka yako.+ Pamenepo udzatukuka+ chifukwa Yehova adzakondweranso nawe kuti akuchitire zabwino, monga mmene anakondwera ndi makolo ako.+ 10 Adzachita zimenezi popeza udzamvera mawu a Yehova Mulungu wako ndi kusunga malamulo ake ndi mfundo zake zolembedwa m’buku ili la chilamulo,+ chifukwa udzabwerera kwa Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse.+

11 “Lamulo limene ndikukupatsa lero si lovuta kwa iwe kulitsatira, ndipo si lapatali.+ 12 Silili kumwamba kuti unene kuti, ‘Ndani adzakwera kumwamba ndi kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’+ 13 Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti unene kuti, ‘Ndani adzawoloka kupita tsidya lina la nyanja kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’ 14 Pakuti mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako+ kuti uwatsatire.+

15 “Taona, ine ndikuika pamaso pako lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+ 16 [Ngati udzamvera malamulo a Yehova Mulungu wako,] amene ndikukupatsa lero ndi kukonda Yehova Mulungu wako,+ kuyenda m’njira zake ndi kusunga malamulo ake,+ mfundo zake ndi zigamulo zake,+ pamenepo udzakhaladi ndi moyo+ ndi kuchulukana. Ndipo Yehova Mulungu wako adzakudalitsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+

17 “Koma mtima wako ukatembenukira kwina ndipo sukumvera,+ moti wanyengeka, n’kugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+ 18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu mutawoloka Yorodano. 19 Ndaika moyo ndi imfa, dalitso+ ndi temberero+ pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu.+ Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+ 20 Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kum’mamatira,+ chifukwa iye ndiye wokupatsani moyo ndi masiku ambiri+ kuti mukhale panthaka imene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzawapatsa.”+

31 Pamenepo Mose anapita ndi kukauza Aisiraeli onse mawu awa, 2 kuti: “Tsopano ndili ndi zaka 120.+ Sindidzaloledwanso kupitiriza ntchito yanga yokutsogolerani,+ pakuti Yehova wandiuza kuti, ‘Suwoloka Yorodano uyu.’+ 3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni.+ Iye ndiye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu, ndipo inu mudzaipitikitse.+ Yoswa ndiye adzakutsogolerani ndi kukuwolotsani,+ monga mmene Yehova wanenera. 4 Ndipo Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo, pamene anawawononga.+ 5 Yehova wapereka mitunduyi kwa inu,+ ndipo muichitire mogwirizana ndi malamulo onse amene ndakupatsani.+ 6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+

7 Pamenepo Mose anaitana Yoswa ndi kumuuza pamaso pa Aisiraeli onse kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa ndiwe amene udzalowetsa anthu awa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzawapatsa.+ Ndipo iwe ndi amene udzawapatsa dzikolo monga cholowa chawo. 8 Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+

9 Pamenepo Mose analemba chilamulo chimenechi+ ndi kuchipereka kwa ansembe, ana a Levi,+ onyamula likasa la pangano la Yehova.+ Anachiperekanso kwa akulu onse a Isiraeli. 10 Ndiyeno Mose anawalamula kuti: “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, pa nthawi yoikidwiratu m’chaka chopuma,+ pachikondwerero cha misasa,+ 11 pamene Aisiraeli onse afika kudzaona nkhope ya Yehova+ Mulungu wanu pamalo amene iye adzasankhe,+ muziwerenga chilamulo ichi pamaso pa Aisiraeli onse m’makutu mwawo.+ 12 Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsere ndi kuphunzira,+ pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu+ ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi. 13 Ana awo amene sadziwa chilamulo ichi azimvetsera,+ ndipo aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse amene mudzakhala panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu,+ mutawoloka Yorodano.”

14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Taona, nthawi ya kufa kwako yayandikira.+ Itana Yoswa, ndipo muime m’chihema chokumanako kuti ndimuike kukhala mtsogoleri.”+ Choncho Mose ndi Yoswa anapita ndi kukaima m’chihema chokumanako.+ 15 Ndiyeno Yehova anaonekera kuchihemako, mumtambo woima njo ngati chipilala, ndipo mtambowo unaima pakhomo la chihema.+

16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo ugona pamodzi ndi makolo ako,+ ndipo anthu awa adzaimirira+ ndi kuchita chiwerewere pakati pawo ndi milungu yachilendo ya m’dziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ ndi kuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ 17 Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+ 18 Koma ine ndidzawabisira nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoipa zonse zimene achita, chifukwa chotembenukira kwa milungu ina.+

19 “Tsopano dzilembereni nyimbo iyi+ ndi kuwaphunzitsa ana a Isiraeli.+ Muiike m’kamwa mwawo kuti nyimbo imeneyi ikhale mboni yanga pamaso pa ana a Isiraeliwo.+ 20 Pakuti ndidzawalowetsa m’dziko limene ndinalumbirira makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Kumeneko iwo adzadya+ ndi kukhuta, ndipo adzatukuka+ ndi kutembenukira kwa milungu ina.+ Adzatumikira milungu imeneyo ndi kundichitira chipongwe, ndipo adzaphwanya pangano langa.+ 21 Ndiyeno masoka ndi zowawa zambiri zikadzawagwera,+ nyimboyi idzawayankha monga mboni, chifukwa siyenera kuchoka pakamwa pa mbadwa zawo, pakuti ndikudziwa mtima+ umene akuyamba kukhala nawo lero ndisanawalowetse m’dziko limene ndawalumbirira.”

22 Chotero Mose analemba nyimboyi pa tsiku limeneli kuti aphunzitse ana a Isiraeli.+

23 Ndiyeno Mulungu anaika Yoswa mwana wa Nuni+ kukhala mtsogoleri, ndipo anamuuza kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetsa ana a Isiraeli m’dziko limene ndawalumbirira,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukhala nawe.”

24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a chilamulo ichi m’buku,+ 25 anayamba kupereka malamulo kwa Alevi onyamula likasa la pangano la Yehova,+ kuti: 26 “Tengani buku ili la chilamulo,+ muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, kuti likhale mboni ya Mulungu yokutsutsani.+ 27 Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga! 28 Sonkhanitsani akulu onse a mafuko anu ndi atsogoleri anu,+ kuti ndilankhule mawu awa m’makutu mwawo, ndipo nditenge kumwamba ndi dziko lapansi kukhala mboni zanga pamaso pawo.+ 29 Pakuti ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zokuwonongetsani+ ndipo mudzapatuka ndi kusiya njira imene ndakulamulani kuyendamo. Pamapeto pake tsoka+ lidzakugwerani, chifukwa mudzachita zoipa pamaso pa Yehova ndi kumulakwira ndi ntchito za manja anu.”+

30 Chotero Mose anayamba kulankhula mawu onse a nyimbo iyi, mpingo wonse wa Isiraeli ukumva,+ ndipo anati:

32 “Tamverani kumwamba inu, ndiloleni ndilankhule.

Ndipo dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.+

 2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,+

Mawu anga adzatsika ngati mame,+

Ngati mvula yowaza pa udzu,+

Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.+

 3 Pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova.+

Vomerezani ukulu wa Mulungu wathu!+

 4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+

Njira zake zonse ndi zolungama.+

Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita chosalungama.+

Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+

 5 Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa,+

Si ana ake, chilemacho n’chawo.+

Iwo ndiwo m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota!+

 6 Kodi mukupitiriza kuchitira Yehova mwa njira imeneyi,+

Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+

Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+

Amene anakupangani ndi kukuchititsani kukhazikika?+

 7 Kumbukirani masiku akale,+

Ganizirani zaka za mibadwomibadwo ya m’mbuyomu.

Funsa bambo ako ndipo akuuza,+

Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.+

 8 Pamene Wam’mwambamwamba anapereka cholowa kwa mitundu,+

Pamene analekanitsa ana a Adamu,+

Anaika malire a anthu+

Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+

 9 Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake.+

Yakobo ndiye gawo la cholowa chake.+

10 Anam’peza m’dziko lachipululu,+

M’chipululu chopanda kanthu, molira zilombo zakutchire.+

Pamenepo anayamba kum’zungulira,+ kum’samalira,+

Kum’teteza monga mwana wa diso lake.+

11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera mwamphamvu chisa chake,

Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,+

Mmene chimatambasulira mapiko ake, ndi kutenga anawo,

N’kuwanyamula pamapiko ake,+

12 Yehova yekha anapitiriza kumutsogolera,+

Ndipo panalibe mulungu wachilendo kuwonjezera pa iye.+

13 Anapitiriza kumuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+

Moti anadya zokolola za m’minda.+

Anapitirizanso kumudyetsa uchi wochokera m’thanthwe,+

Ndi mafuta ochokera m’mwala wa nsangalabwi.+

14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ng’ombe ndi mkaka wa nkhosa,+

Pamodzi ndi mafuta a nkhosa.

Anamudyetsa nkhosa zamphongo za ku Basana, mbuzi zamphongo,+

Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa ngati mafuta okuta impso.+

Ndipo anali kumwa magazi a mphesa monga vinyo.+

15 Yesuruni*+ atayamba kunenepa, anayamba kupanduka.+

Iwe wanenepa, wakulupala, wakhuta mopitirira muyezo.+

Pamenepo iye anasiya Mulungu amene anam’panga,+

Ndi kunyoza Thanthwe+ la chipulumutso chake.

16 Anayamba kuputa nsanje+ yake ndi milungu yachilendo.+

Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+

17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+

Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+

Milungu yatsopano yongobwera kumene,+

Imene makolo anu akale sanaidziwe.

18 Munaiwala Thanthwe limene linakuberekani,+

Ndipo munayamba kuiwala Mulungu amene anachititsa kuti mukhalepo kudzera mwa zowawa za pobereka.+

19 Yehova ataona zimenezi anayamba kuwanyoza,+

Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakaziwo anam’sautsa.

20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+

Ndione kuti ziwathera bwanji.

Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+

Ana osakhulupirika.+

21 Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+

Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+

Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+

Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+

22 Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+

Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+

Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+

Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+

23 Ndidzawonjezera masoka awo,+

Mivi yanga ndidzaithera pa iwo.+

24 Adzalefuka ndi njala+ ndi kuwonongeka ndi matenda otentha thupi koopsa,+

Ndi chiwonongeko chowawa.+

Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali,+

Pamodzi ndi njoka zapoizoni za m’fumbi.+

25 Kunja lupanga lidzawasandutsa anamfedwa,+

Ndipo mkati mwa nyumba, mantha adzawasandutsa anamfedwa.+

Zimenezi zidzawaphera anyamata ndi anamwali,+

Mwana woyamwa pamodzi ndi munthu wa imvi.+

26 Ndikananena kuti: “Ndidzawabalalitsa,+

Ndidzachititsa anthu kuti asatchule n’komwe za iwo,”+

27 Ngati ndikanati sindikuopa kusautsidwa ndi mdani,+

Kuti adani awo angamve molakwa,+

Kutinso anganene kuti: “Dzanja lathu lapambana,+

Ndipo si Yehova amene wachita zonsezi.”+

28 Pakuti iwo ndi mtundu wopanda nzeru,+

Ndipo ndi osazindikira.+

29 Akanakhala anzeru,+ akanaganizira mozama zimenezi.+

Akanalingalira kuti ziwathera bwanji.+

30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,

Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+

N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+

Komanso ngati Yehova atawapereka.

31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,+

Ndipo adani athu angavomereze zimenezi.+

32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,

Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+

Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha,

Ndipo ndi zowawa.+

33 Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka zikuluzikulu,

Ndiponso ndi poizoni wakupha wa mamba.+

34 Kodi sindinasunge zimenezi,

Ndi kuziikira chidindo m’nkhokwe yanga?+

35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+

Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+

Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera.

Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake.

37 Pamenepo iye adzati, ‘Ili kuti milungu yawo,+

Thanthwe limene anathawirako,+

38 Milungu imene inali kudya mafuta a nsembe zawo,+

Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+

Ibwere kudzakuthandizani.+

Ikhaletu malo anu obisalamo.+

39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+

Ndipo palibe milungu ina pamodzi ndi ine.+

Ndimapha ndiponso ndimapereka moyo.+

Ndavulaza koopsa,+ ndipo ine ndidzachiritsa,+

Palibe aliyense wonditsomphola m’dzanja langa.+

40 Ndikukweza dzanja langa kumwamba polumbira,+

Ndipo ndikunena kuti: “Pali ine, Mulungu wamoyo wosatha,”+

41 Ndikanoladi lupanga langa lonyezimira,+

Dzanja langa likagwira chiweruzo,+

Ndidzalipsira adani anga,+

Ndipo ndidzabwezera chilango kwa odana nane kwambiri.+

42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,+

Magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa.

Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,+

Pamodzi ndi mitu ya atsogoleri a adani.’+

43 Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake,+

Pakuti adzabwezera magazi a atumiki ake,+

Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+

Nadzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”

44 Pamenepo Mose anabwera ndi kulankhula mawu onse a nyimbo iyi m’makutu mwa anthu onse,+ iye pamodzi ndi Hoseya* mwana wa Nuni.+ 45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46 anapitiriza kuwauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse amene ndikulankhula mokuchenjezani lero,+ ndipo muuze ana anu kuti aonetsetse kuti akuchita zimene mawu onse a chilamulo ichi akunena.+ 47 Pakuti amenewa si mawu opanda pake kwa inu,+ chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.+ Mwa kutsatira mawu amenewa mudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu, mutawoloka Yorodano.”+

48 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49 “Kwera m’phiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili m’dziko la Mowabu, moyang’anana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli kuti likhale lawo.+ 50 Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake. 51 Izi zili choncho chifukwa anthu inu munachita mosakhulupirika kwa ine+ pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, m’chipululu cha Zini. Ndiponso chifukwa chakuti anthu inu simunandilemekeze pakati pa ana a Isiraeli.+ 52 Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli.”+

33 Tsopano ili ndi dalitso+ limene Mose, munthu wa Mulungu woona,+ anadalitsa nalo ana a Isiraeli iye asanafe. 2 Ndipo anati:

“Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+

Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+

Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+

Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+

Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+

 3 Iye analinso kukonda anthu ake.+

Oyera awo onse ali m’manja mwanu.+

Iwowa anakhala pansi, pamapazi panu.+

Anayamba kulandira ena mwa mawu anu.+

 4 (Mose anatipatsa chilamulo,+

Chimene mpingo wa Yakobo uli nacho monga chawo.)+

 5 Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+

Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+

Chiwerengero chonse cha mafuko a Isiraeli.+

 6 Rubeni akhale ndi moyo, asafe ayi,+

Ndipo anthu ake asakhale ochepa.”+

7 Popitiriza, iye anapereka dalitso lotsatirali kwa Yuda,+ kuti:

“Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+

M’bweretseni kwa anthu ake.

Manja ake amenya nkhondo pofuna kulanditsa zinthu zake.

Mukhaletu mthandizi wake kwa adani ake.”+

8 Ndipo kwa Levi anati:+

“Tumimu ndi Urimu+ wanu ndizo za munthu wokhulupirika kwa inu,+

Amene munamuyesa pa Masa.+

Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a Meriba.+

 9 Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinawaone.’

Ngakhale abale ake sanawavomereze,+

Ndipo ana ake sanawadziwe.

Pakuti anasunga mawu anu,+

Ndipo anapitiriza kusunga pangano lanu.+

10 Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu,+

Ndi Isiraeli m’chilamulo chanu.+

Azipereka nsembe zofukiza kuti muzinunkhiza fungo lake,+

Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+

11 Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,+

Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.+

Muvulaze koopsa ziuno za amene akumuukira,+

Ndi amene amadana naye kwambiri, kuti asamuukire.”+

12 Kwa Benjamini anati:+

“Wokondedwa+ wa Yehova akhale m’chitetezo cha Mulungu,+

Pamene akumutchinjiriza tsiku lonse,+

Ndipo iye akhale pakati pa mapewa ake.”+

13 Ndipo kwa Yosefe anati:+

“Dziko lake lipitirize kudalitsidwa ndi Yehova.+

Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba, mame,+

Ndi madzi akuya a pansi pa nthaka.+

14 Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,+

Ndi zinthu zabwino kwambiri, zokolola za miyezi yosiyanasiyana,+

15 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa, za m’mapiri a kum’mawa,+

Ndi zinthu zabwino kwambiri za m’mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.

16 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+

Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera m’chitsamba chaminga.+

Zimenezi zikhale pamutu pa Yosefe,+

Paliwombo pa munthu wopatulidwa pakati pa abale ake.+

17 Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ng’ombe wamphongo woyamba kubadwa,+

Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+

Nyanga zimenezo adzakankha nazo anthu.+

Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi.

Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+

Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.”

18 Kwa Zebuloni anati:+

“Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,+

Ndiponso iwe Isakara, m’mahema ako.+

19 Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri.

Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.+

Pakuti adzayamwa chuma chochuluka cha m’nyanja,+

Ndi chuma chobisika cha mumchenga.”

20 Ndipo kwa Gadi anati:+

“Wodala ndi iye wofutukula malire a dera la Gadi.+

Iye adzakhala ngati mkango,+

Ndipo adzakhadzula dzanja, adzang’amba mutu paliwombo.+

21 Adzatenga gawo labwino kwambiri kukhala lake,+

Pakuti gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+

Ndipo atsogoleri a anthu adzasonkhana.

Iye adzachitadi chilungamo cha Yehova,

Ndi zigamulo zokhudza Isiraeli.”

22 Kwa Dani anati:+

“Dani ndi mwana wa mkango.+

Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+

23 Ndipo kwa Nafitali anati:+

“Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa ndi Yehova,

Ndipo madalitso Ake amuchulukira.

Tenga chigawo cha kumadzulo ndi kum’mwera.”+

24 Kwa Aseri anati:+

“Aseri ndi wodalitsidwa ndi ana aamuna.+

Akhale wovomerezeka ndi abale ake,+

Woponda phazi lake m’mafuta.+

25 Chitsulo ndi mkuwa ndizo zokhomera chipata chako,+

Udzayenda mtima uli phee, masiku onse a moyo wako.

26 Palibe wina wofanana ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+

Amene amayenda m’mlengalenga pokuthandiza,+

Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+

27 Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo,+

Ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.+

Adzapitikitsa mdani pamaso pako,+

Ndipo adzanena kuti, ‘Awononge!’+

28 Isiraeli adzakhala motetezeka,+

Kasupe wa Yakobo adzakhala mosatekeseka,+

M’dziko lokhala ndi chakudya ndi vinyo watsopano.+

Ndipo kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+

29 Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+

Ndani angafanane ndi iwe,+

Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+

Chishango chako chokuthandiza,+

Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+

Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+

Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+

34 Ndiyeno Mose anachoka m’chipululu cha Mowabu kupita m’phiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyang’anana ndi Yeriko.+ Pamenepo Yehova anayamba kumuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+ 2 Anamuonetsanso dziko lonse la Nafitali, dziko la Efuraimu ndi la Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kunyanja ya kumadzulo.+ 3 Anamuonetsa Negebu+ ndi Chigawo*+ cha Yorodano, chigwa cha ku Yeriko, mzinda wa mitengo ya kanjedza,+ mpaka ku Zowari.+

4 Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Dziko lija ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbewu yako’+ ndi limeneli. Ndakuonetsa kuti ulione ndi maso ako chifukwa sudzawoloka kukalowa m’dzikolo.”+

5 Kenako Mose mtumiki wa Yehova+ anafera pamenepo m’dziko la Mowabu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula.+ 6 Iye anamuika m’manda m’chigwa, m’dziko la Mowabu moyang’anana ndi Beti-peori,+ ndipo palibe amene akudziwa manda ake kufikira lero.+ 7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120.+ Diso lake silinachite mdima+ ndipo anali adakali ndi mphamvu.+ 8 Ana a Isiraeli analira Mose m’chipululu cha Mowabu masiku 30.+ Ndiyeno masiku onse olira maliro a Mose anatha.

9 Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru,+ pakuti Mose anaika manja ake pa iye.+ Choncho ana a Isiraeli anayamba kumumvera ndipo iwo anayamba kuchita monga momwe Yehova analamulira Mose.+ 10 Koma mu Isiraeli simunakhalebe mneneri aliyense wofanana ndi Mose,+ amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso,+ 11 amene anachita zizindikiro ndi zozizwitsa zonse zimene Yehova anam’tuma kukachita m’dziko la Iguputo kwa Farao, kwa atumiki ake onse ndi m’dziko lake lonse.+ 12 Simunakhalebe mneneri amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa ndi dzanja lake lamphamvu, ngati zimene Mose anachita pamaso pa Aisiraeli onse.+

Kutanthauza m’chaka cha 40 atachoka ku Iguputo.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Dzinali limatanthauza “Midzi ya Mahema ya Yairi.”

“Kinereti” ndi dzina loyambirira la Nyanja ya Galileya.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 34:28.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:4.

Kapena kuti “iye ndi Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”

Kapena kuti “zikumbutso.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:4.

Kapena kuti “Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”

Kapena kuti “wolanga ana, m’badwo wachitatu ndi m’badwo wachinayi.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:13.

Pano, “Mawu” akutanthauza mawu olamula, kapena kuti malamulo. Onani Eks 34:28.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti “Yehova ndi Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi [kapena, pali Yehova mmodzi].”

Mawu ake enieni, “pakati pa maso ako.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Dzina lakuti “Masa” limatanthauza “Kuyesa; Mayesero.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 34:28.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kutanthauza kuti, kuthirira pogwiritsa ntchito mapazi, mwina mwa kupalasa gudumu lotungira madzi kapena mwa kutsegula ndi kutseka ngalande ndi mapazi.

Mawu ake enieni, “Ine,” kutanthauza Mulungu.

Ena amati “wonzuna.”

Onani mawu a m’munsi pa De 6:8.

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Mawu akuti “kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa” angalembedwenso kuti “kanthu kalikonse kotembereredwa.”

Kapena kuti “kumeta mpala pachipumi panu.”

Mawu ake enieni, “munthu amene si Mwisiraeli.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani Zakumapeto 13.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Mawu ake enieni, “kudutsitsa pamoto.”

Onani mawu a m’munsi pa Le 19:26.

Mawu akuti ‘kulodza’ kapena ‘kuchisa’ amatanthauza kupweteka kapena kulepheretsa munthu kuchita chinachake mwa njira ya matsenga.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kapena kuti “patsindwi.”

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Kutanthauza mnyamata wosungidwira kugonedwa ndi amuna.

Mawu awa angatanthauze munthu amene makamaka amagona mnyamata kumbuyo.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Ena amati “matenda a mdidi,” kapena “matenda otuluka thumbo.”

Munthu wosasatitsidwa ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.

Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.

Onani Zakumapeto 5.

Dzina lakale la Yoswa.

Onani mawu a m’munsi pa De 32:15.

Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena