Yoswa
1 Mose mtumiki wa Yehova atamwalira, Yehova analankhula ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, mtumiki+ wa Mose, kuti: 2 “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu ndi kulowa m’dziko limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+ 3 Malo alionse amene phazi lanu lidzapondapo ndidzawapereka ndithu kwa inu, monga mmene ndinalonjezera kwa Mose.+ 4 Dziko lanu lidzayambira kuchipululu ndi ku Lebanoni uyu mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu, kolowera dzuwa.+ 5 Palibe amene adzatha kulimbana nawe masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe+ monga mmene ndinakhalira ndi Mose, sindidzakutaya kapena kukusiya ngakhale pang’ono.+ 6 Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ pakuti ndiwe amene utsogolere anthuwa kuti akalandire dziko+ limene ndinalumbirira makolo awo kuti ndidzawapatsa.+
7 “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula.+ Malamulowo usawasiye ndi kupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uchite mwanzeru kulikonse kumene udzapitako.+ 8 Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako,+ uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo.+ Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.+ 9 Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+
10 Tsopano Yoswa analamula akapitawo a anthuwo kuti: 11 “Pitani mumsasa wonsewu, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani ndi kutenga zonse zofunikira, chifukwa pakapita masiku atatu kuchokera lero, mudzawoloka Yorodano uyu, ndi kulowa m’dzikolo kuti mukalilande, dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.’”+
12 Kenako, Yoswa analankhula ku fuko la Rubeni, ku fuko la Gadi, ndi ku hafu ya fuko la Manase, kuti: 13 “Mukumbukire mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani,+ akuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndipo wakupatsani dziko ili. 14 Akazi anu ndi ana anu aang’ono atsale limodzi ndi ziweto zanu m’dziko lino limene Mose anakupatsani, tsidya lino la Yorodano.+ Koma amunanu, mudzawoloka patsogolo pa abale anu, mutafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ Inuyo, amuna nonse amphamvu ndi olimba mtima,+ muwoloke kuti mukawathandize abale anu. 15 Ndipo Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, monga waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakalanda dziko limene Yehova Mulungu akuwapatsa,+ m’pamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kudziko la cholowa chanu limene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani,+ tsidya lino la Yorodano, kum’mawa kuno.’”+
16 Amunawo anayankha Yoswa kuti: “Zonse zimene mwatilamula tichita, ndipo kulikonse kumene mungatitumize tipita.+ 17 Monga tinamvera Mose m’chilichonse, tidzakhalanso omvera kwa inu. Yehova Mulungu wanu akhale nanu+ mmene anakhalira ndi Mose.+ 18 Munthu aliyense wopandukira malamulo anu,+ ndi wosamvera mawu anu pa chilichonse chimene mungamulamule, ameneyo aphedwe.+ Inuyo mukhale wolimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.”+
2 Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatumiza amuna awiri mwachinsinsi monga azondi kuchokera ku Sitimu.+ Anawalangiza kuti: “Pitani, mukazonde dzikolo ndi mzinda wa Yeriko.” Chotero iwo anapita n’kukafika kunyumba ya mayi wina yemwe anali hule, dzina lake Rahabi,+ n’kukhala kumeneko. 2 Kenako mfumu ya Yeriko inauzidwa kuti: “Taonani! Amuna ochokera kwa ana a Isiraeli alowa mumzinda wathu usiku uno kudzafufuza dziko lathu.” 3 Mfumu ya Yeriko itamva zimenezo inatumiza anthu kukauza Rahabi kuti: “Tulutsa amuna amene abwera kwa iwe, omwe alowa m’nyumba mwako, chifukwa abwera kudzafufuza dziko lathu lonse lino.”+
4 Pamenepo mayiyo anatenga amuna awiriwo n’kuwabisa. Kenako anayankha kuti: “Inde, amunawo anabweradi kwa ine, koma sindinadziwe kuti achokera kuti. 5 Ndipo amunawo atuluka usiku uno nthawi yotseka chipata+ itayandikira. Koma ine sindikudziwa kumene alowera. Fulumirani! Athamangireni! Muwapeza amenewo.” 6 (Koma iye anali atawatengera padenga,*+ ndi kuwabisa pansi pa mapesi a fulakesi* padengapo.) 7 Amunawo anathamangira azondi aja, cha kowolokera mtsinje wa Yorodano.+ Ndipo atangotuluka pachipata cha mzinda, nthawi yomweyo chipatacho chinatsekedwa.
8 Azondi aja asanagone, Rahabi anakwera padenga pamene iwo anali. 9 Ndipo iye anauza amunawo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.+ Ife tagwidwa ndi mantha chifukwa cha inu,+ ndipo anthu a dziko lino ataya mtima chifukwa chokuopani.+ 10 Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano. 11 Titangomva zimenezi, mitima yathu inayamba kusungunuka ndi mantha,+ ndipo mpaka pano palibe aliyense amene akulimba mtima, chifukwa choopa inu.+ Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa kumwamba ndi padziko lapansi.+ 12 Tsopano, chonde lumbirani kwa ine pali Yehova,+ kuti chifukwa choti ndakusonyezani kukoma mtima kosatha, inunso mudzasonyeza anthu a m’nyumba ya bambo anga+ kukoma mtima kosatha, ndipo mundipatse chizindikiro chodalirika.+ 13 Musadzaphe bambo anga,+ mayi anga, abale anga ndi alongo anga, limodzi ndi mabanja awo. Mudzatisiye amoyo.”+
14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+ 15 Pambuyo pake, mkaziyo anatulutsa amunawo powatsitsa ndi chingwe pawindo, pakuti mpanda wa mzindawo unalinso khoma* la nyumba yake, ndipo nyumba yakeyo inali pampandapo.+ 16 Iye anauza amunawo kuti: “Muthawire kumapiri kuti amene akukusakani aja asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu, mpaka iwo atabwerako, kenako muzikapita kwanu.”
17 Amunawo anayankha kuti: “Tisungadi pangano limene iwe watilumbiritsa, ndipo tidzakhala opanda mlandu.+ 18 Tikubwera ndithu m’dziko muno! Chingwe chofiira ichi uchimangirire pawindo limene watitulutsirapo. Bambo ako ndi mayi ako, abale ako ndi alongo ako, ndi onse a m’nyumba ya bambo ako, uwasonkhanitse kuti adzakhale m’nyumba mwako.+ 19 Aliyense amene adzatuluke pakhomo la nyumba yako kupita panja,+ magazi ake adzakhala pamutu pake. Ife tidzakhala opanda mlandu. Koma ngati aliyense amene adzakhalebe limodzi nawe m’nyumbamu adzaphedwe, magazi ake adzakhale pamutu pathu. 20 Ndipo ngati ungaulule nkhaniyi,+ tidzakhalanso opanda mlandu pa pangano limene watilumbiritsali.” 21 Pamenepo mkaziyo anati: “Zikhale monga mwanenera.”
Atatero anawauza kuti azipita, ndipo iwo ananyamuka. Kenako mkaziyo anamanga chingwe chofiira chija pawindopo. 22 Chotero amuna aja anatuluka, nakafika kumapiri kuja. Anakhala kumeneko masiku atatu mpaka owasaka aja atabwerera. Owasakawo anawafunafuna mumsewu uliwonse, koma sanawapeze. 23 Amuna aja anatsika m’mapirimo, ndipo atawoloka mtsinje, anakafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Atafika, anayamba kum’fotokozera zonse zimene zinawachitikira. 24 Iwo anauza Yoswa kuti: “Yehova wapereka dziko lonselo m’manja mwathu.+ Ndipo anthu onse a m’dzikomo akuchita mantha chifukwa cha ife.”+
3 M’mamawa kutacha, Yoswa ndi ana a Isiraeli onse ananyamuka ku Sitimu.+ Anayenda mpaka kukafika kumtsinje wa Yorodano, kumene anagona usiku umenewo asanawoloke.
2 Patatha masiku atatu aja,+ akapitawo+ a anthuwo anapita mumsasa, 3 ndipo anauza anthuwo kuti: “Mukangoona likasa la pangano la Yehova Mulungu wanu litanyamulidwa ndi ansembe achilevi,+ musamuke pamalo panu ndi kulitsatira, 4 koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi likasalo pakhale mtunda wokwana mikono* pafupifupi 2,000.+ Mukatero, mudzadziwa njira yoyenera kuyendamo, pakuti kumeneko simunayambe mwapitako.”
5 Tsopano Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mudziyeretse,+ chifukwa mawa Yehova achita zodabwitsa pakati panu.”+
6 Kenako Yoswa anauza ansembe kuti: “Nyamulani likasa la pangano,+ muyende nalo patsogolo pa anthuwa.” Chotero ansembewo ananyamula likasa la panganolo, n’kumayenda nalo patsogolo pa anthuwo.
7 Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndiyamba kukukuza pamaso pa Aisiraeli onse,+ n’cholinga choti adziwe kuti monga mmene ndinakhalira ndi Mose,+ ndidzakhalanso ndi iwe.+ 8 Tsopano lamula+ ansembe onyamula likasa la pangano. Uwauze kuti: ‘Mukakangofika kumtsinje wa Yorodano, mukalowe m’madzimo ndi kuima+ m’mphepete mwa mtsinjewo.’”
9 Ndiyeno Yoswa anauza ana a Isiraeli kuti: “Bwerani kuno, mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.” 10 Atafika, Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo alidi pakati panu.+ Mudziwanso kuti iye adzathamangitsadi pamaso panu Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+ 11 Taonani! Likasa la pangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi liyenda patsogolo panu kulowa mumtsinje wa Yorodano. 12 Tsopano tengani amuna 12 m’mafuko a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+ 13 Zimene zichitike n’zakuti, mapazi a ansembe onyamula likasa la Yehova, Ambuye wa dziko lonse lapansi, akangoponda m’madzi, madzi a mtsinje wa Yorodanowo aduka. Madzi otsika kuchokera kumtunda aima n’kukhala damu limodzi.”+
14 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Anthuwo anachotsa mahema awo, n’kunyamuka. Anayandikira Yorodano kuti awoloke, ndipo ansembe onyamula likasa+ la pangano anali patsogolo pawo. 15 Onyamula Likasawo atangofika kumtsinje wa Yorodano, n’kuponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo (mtsinje wa Yorodano unali kusefukira+ nyengo yonse yokolola), 16 madzi otsika kuchokera kumtunda anayamba kuima. Madziwo anakwera m’mwamba, ndipo anasefukira n’kupanga damu,+ limene linafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani.+ Koma madzi omwe anali kutsikira kunyanja ya Araba, imene ndiyo Nyanja Yamchere,+ anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anaduka, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko. 17 Ansembe onyamula likasa la pangano la Yehova anangoima chilili panthaka youma+ pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe choncho pamene Aisiraeli onse anali kuwoloka panthaka youmayo,+ kufikira mtundu wonse unatha kuwoloka mtsinje wa Yorodano.
4 Mtundu wonse utangotha kuwoloka mtsinje wa Yorodano,+ Yehova anauza Yoswa kuti: 2 “Tenga amuna 12 pakati pa anthuwa, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+ 3 Uwalamule kuti, ‘Pitani pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene ansembe anaimapo chilili,+ mukanyamulepo miyala 12.+ Muisenze ndi kukaiika kumene mugone+ usiku wa lero.’”
4 Choncho Yoswa anaitana amuna 12+ amene anawasankha pakati pa ana a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse. 5 Ndipo anawauza kuti: “Dutsani kutsogolo kwa likasa la Yehova Mulungu wanu, mukafike pakati pa mtsinje wa Yorodano. Aliyense akanyamule mwala umodzi paphewa pake, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Isiraeli. 6 Miyala imeneyo idzakhala chizindikiro pakati panu.+ Ana anu akamadzafunsa m’tsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 7 Muzidzawauza kuti, ‘N’chifukwa chakuti madzi a mumtsinje wa Yorodano anadukana pamaso pa likasa la pangano la Yehova.+ Likasalo litadutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinje wa Yorodanowo anadukana, ndipo miyala imeneyi ndi chikumbutso cha zimenezo kwa ana a Isiraeli mpaka kalekale.’”*+
8 Chotero ana a Isiraeliwo anachita monga mmene Yoswa anawalamulira. Anapita pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo anakanyamula miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Isiraeli,+ monga mmene Yehova analamulira Yoswa. Ananyamula miyalayo ndi kukaiika kumalo awo ogona.+
9 Panalinso miyala ina 12 imene Yoswa anaisanjikiza pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene anaimapo+ ansembe onyamula likasa la pangano. Miyalayo ilipo mpaka lero.
10 Ansembe onyamula Likasawo, anaimabe chiimire pakati+ pa mtsinje wa Yorodano, kufikira zitachitika zonse zimene Yehova analamula Yoswa kuti auze anthuwo, mogwirizana ndi zonse zimene Mose analamula Yoswa.+ Ansembewo ali chiimire choncho, anthuwo anawoloka mtsinjewo mofulumira.+ 11 Anthu onse atangotha kuwoloka, likasa+ la Yehova linawoloka litanyamulidwa ndi ansembewo pamaso pa anthuwo. 12 Ana a Rubeni ndi ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase,+ anawoloka pamaso pa ana a Isiraeli atafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo,+ monga mmene Mose anawauzira.+ 13 Amuna onyamula zida okwanira pafupifupi 40,000, anawoloka pamaso pa Yehova kukamenya nkhondo m’chipululu cha Yeriko.
14 Pa tsikuli, Yehova anachititsa Yoswa kukhala wamkulu m’maso mwa Aisiraeli onse,+ ndipo anayamba kumuopa monga mmene anaopera Mose masiku onse a moyo wake.+
15 Yehova anauza Yoswa kuti: 16 “Lamula ansembe onyamula likasa la umboni+ kuti atuluke mumtsinje wa Yorodano.” 17 Chotero Yoswa analamula ansembewo, kuti: “Tulukani mumtsinje wa Yorodano.” 18 Ansembe onyamula likasa+ la pangano la Yehova atatuluka pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo mapazi+ awo ataponda kumtunda, madzi a mtsinjewo anayamba kubwerera mwakale, ndipo anasefukira+ mbali zonse ngati poyamba.
19 Anthuwo anawoloka mtsinje wa Yorodano pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, ndipo anakamanga msasa ku Giligala,+ kumalire a kum’mawa kwa Yeriko.
20 Miyala 12 imene iwo anaitenga mumtsinje wa Yorodano ija, Yoswa anaisanjikiza ku Giligala.+ 21 Kenako anauza ana a Isiraeli kuti: “Ana anu akamadzafunsa abambo awo m’tsogolomu kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22 Muzidzawauza ana anuwo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodanowu panthaka youma.+ 23 Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pawo, kufikira iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo pamaso pathu, mpaka tonse titawoloka.+ 24 Yehova anachita zimenezi kuti mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi idziwe kuti dzanja lake+ ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muzimuopadi Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”+
5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+
2 Pa nthawi imeneyo, Yehova anauza Yoswa kuti: “Panga timipeni tamiyala kuti udule khungu+ la ana a Isiraeli kachiwiri.” 3 Chotero Yoswa anapanga timipeni tamiyala, ndipo anadula khungu la ana a Isiraeli. Zimenezi zinachitikira ku Gibeyati-haaraloti.+ 4 Yoswa anadula khungu la ana a Isiraeliwo chifukwa chakuti anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amuna onse otha kupita kunkhondo, anali atafera+ m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo. 5 Anthu onse amene anatuluka mu Iguputo anali odulidwa. Koma onse amene anabadwira m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo, sanadulidwe. 6 Ana a Isiraeliwo anayenda m’chipululu zaka 40,+ mpaka amuna onse otha kupita kunkhondo amene anatuluka mu Iguputo atatha, amene sanamvere mawu a Yehova. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 7 Iye analowetsa m’dzikomo ana awo m’malo mwa makolowo.+ Ana amenewa Yoswa anawadula khungu, chifukwa sanadulidwe pa nthawi imene anali pa ulendo.
8 Atamaliza kuchita mdulidwe pamtundu wonsewo, anthuwo anakhala m’malo awo mumsasa mpaka atachira.+
9 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndachotsa chitonzo cha Iguputo pa inu.”+ Chotero malowo anayamba kuwatchula kuti Giligala,+ kufikira lero.
10 Ana a Isiraeliwo anakhalabe ku Giligala. Anachita pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ ali m’chipululu cha Yeriko. 11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za m’dzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda chofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene ana a Isiraeli anadya zokolola za m’dzikomo. Kuyambira pamenepo, mana sanagwenso pakati pa ana a Isiraeli.+ Chotero, chaka chimenechi n’chimene iwo anayamba kudya zokolola za m’dziko la Kanani.+
13 Tsiku lina Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima potero patsogolo pake, ali ndi lupanga m’dzanja lake.+ Pamenepo Yoswa anayandikira munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” 14 Munthuyo anayankha kuti: “Iyayi, koma ine pokhala kalonga wa gulu lankhondo la Yehova, tsopano ndabwera.”+ Yoswa atamva mawu amenewo, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.” 15 Ndiyeno kalonga wa gulu lankhondo la Yehovayo anauza Yoswa kuti: “Vula nsapato zako, chifukwa malo amene waimapowo ndi oyera.” Nthawi yomweyo, Yoswa anavula nsapato zake.+
6 Mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha ana a Isiraeli. Palibe amene anali kutuluka kapena kulowa mumzindawo.+
2 Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Taona! Mzinda wa Yeriko ndaupereka m’manja mwako, pamodzi ndi mfumu yake ndi asilikali ake amphamvu ndi olimba mtima.+ 3 Tsopano, amuna ankhondo nonsenu, mugube kuzungulira mzindawu kamodzi. Muchite zimenezi kwa masiku 6. 4 Ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa atanyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo. Pa tsiku la 7 mudzagube kuzungulira mzindawo maulendo 7, ansembewo akuliza malipenga.+ 5 Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mfuu yankhondo mwamphamvu,+ ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.”
6 Chotero Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe+ n’kuwauza kuti: “Nyamulani likasa la pangano,+ ndipo ansembe 7 aziyenda patsogolo pa likasa+ la Yehovalo. Ansembewo atenge malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo.” 7 Anauzanso asilikaliwo kuti: “Nyamukani, mukagube kuzungulira mzindawo. Gulu la asilikali onyamula zida zankhondo+ likhale patsogolo pa likasa la Yehova.” 8 Monga Yoswa ananenera, ansembe 7 ananyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa pamaso pa Yehova. Iwo anatsogola akuliza malipenga awo, ndipo likasa la pangano la Yehova linali kuwatsatira pambuyo pawo. 9 Gulu la asilikali onyamula zida linali kuyenda patsogolo pa ansembe oimba malipenga, pamene gulu lina la asilikali linali kubwera pambuyo+ pa Likasa, kwinaku malipenga akuimbidwa mosalekeza.
10 Yoswa analamula asilikaliwo+ kuti: “Musafuule kapena kulankhula kanthu, ndipo pakamwa panu pasatuluke mawu alionse kufikira tsiku limene ndidzakuuzani kuti, ‘Fuulani!’ Pamenepo mudzafuule.”+ 11 Chotero iye atalamula, likasa la Yehova linazungulira mzindawo kamodzi, asilikaliwo akuguba nalo. Pambuyo pake, iwo anapita kumsasa ndipo anakhala kumeneko usiku wonse.
12 Tsiku lotsatira, Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri,+ ndipo ansembe ananyamula likasa+ la Yehova. 13 Ansembe 7 onyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa, omwe anali kukhala patsogolo pa likasa la Yehova, anali kuyenda akuliza malipenga mosalekeza. Patsogolo pawo panali gulu la asilikali onyamula zida, ndipo pambuyo pa likasa la Yehova panali kubwera asilikali ena, malipenga akulira mosalekeza.+ 14 Iwo anagubanso kuzungulira mzindawo kamodzi pa tsiku lachiwirili. Atamaliza kuzungulira anabwerera kumsasa. Anachita zimenezi kwa masiku 6.+
15 Pa tsiku 7, anadzuka m’mawa kutangoyamba kucha, ndipo anaguba kuzungulira mzindawo monga anali kuchitira. Pa tsiku la 7 limeneli, anazungulira mzindawo maulendo 7.+ 16 Pa ulendo wa 7 wozungulira mzindawo, ansembe aja analiza malipenga awo, ndipo Yoswa anauza asilikaliwo kuti: “Fuulani!+ Pakuti Yehova wakupatsani mzindawu.+ 17 Mzindawu wapatulidwa kuti uwonongedwe,+ pakuti mzindawu limodzi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova. Rahabi+ yekha, hule uja, musamuphe. Mum’siye ndi moyo, iye pamodzi ndi onse amene ali naye m’nyumba mwake, chifukwa iye anabisa azondi amene tinawatuma.+ 18 Koma zinthu zoyenera kuwonongedwa musamale nazo,+ kuopera kuti mungazikhumbire+ n’kutengako zinthuzo,+ n’kuchititsa msasa wa Isiraeli nawonso kukhala chinthu choyenera kuwonongedwa ndi kunyanyalidwa.+ 19 Siliva, golide, ndi zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, zonse n’zopatulika kwa Yehova.+ Ziyenera kupita ku chuma cha Yehova.”+
20 Ansembe aja ataliza malipenga awo,+ asilikaliwo anafuula. Atangomva kulira kwa malipenga, anayamba kufuula mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wa mzindawo unayamba kugwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko, ndi kulanda mzindawo. 21 Aliyense amene anali mumzindawo anamupha ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, anyamata ndi nkhalamba zomwe. Anaphanso ng’ombe, nkhosa, ndi abulu.+
22 Ndiyeno Yoswa anauza amuna awiri aja amene anakazonda dzikolo, kuti: “Pitani kunyumba kwa mayi uja, hule uja, mukam’tulutse limodzi ndi onse amene ali naye, monga momwe munalumbirira kwa iye.”+ 23 Chotero, anyamata amene anakazonda dziko aja, anapita kukatulutsa Rahabi, bambo ake, mayi ake, alongo ake, ndi onse amene anali naye. Anatulutsa achibale ake onse,+ ndipo anawapatsa malo kunja kwa msasa wa Isiraeli.
24 Atatero, anatentha ndi moto mzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo.+ Koma siliva, golide, zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, anazipereka kuti zipite ku chuma cha nyumba ya Yehova.+ 25 Ndipo Rahabi hule uja, limodzi ndi anthu a m’nyumba ya bambo ake, ndi onse amene anali naye, Yoswa sanawaphe.+ Kufikira lero, mayiyo akukhalabe pakati pa Aisiraeli,+ chifukwa anabisa anyamata amene Yoswa anawatuma kukazonda Yeriko.+
26 Ndiyeno pa nthawiyo, Yoswa analumbira kuti: “Adzakhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zake za pachipata, mwana wake wotsiriza adzafe.”+
27 Chotero Yehova anakhaladi ndi Yoswa,+ ndipo mbiri yake inamveka padziko lonse lapansi.+
7 Kenako, ana a Isiraeli anachimwa mwa kuphwanya lamulo lokhudza zinthu zoyenera kuwonongedwa. Anachimwa pamene Akani+ mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatengako zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakwiya kwambiri ndi ana a Isiraeli.+
2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni,+ kum’mawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani kumeneko, mukazonde dzikolo.” Amunawo anapita, n’kukazonda dziko la Ai.+ 3 Amunawo atabwerako anauza Yoswa kuti: “Musachite kutumiza anthu onse kumeneko. Mungotumiza amuna pafupifupi 2,000 kapena pafupifupi 3,000, kuti akakanthe Ai. Musatopetse anthu onse n’kupita kumeneko, pakuti kuli anthu ochepa.”
4 Choncho amuna pafupifupi 3,000 okha anapita kumeneko, koma anathawa popitikitsidwa ndi amuna a ku Ai.+ 5 Ndipo amuna a ku Aiwo anapha amuna achiisiraeli pafupifupi 36. Anawathamangitsabe+ kuchokera kuchipata mpaka ku Sebarimu, n’kupitiriza kuwapha mpaka pamalo otsetsereka. Zitatero, mitima ya Aisiraeli onse inasungunuka ndi mantha.+
6 Yoswa ataona zimenezi anang’amba malaya ake. Kenako anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ patsogolo pa likasa la Yehova, mpaka madzulo. Anachita zimenezi pamodzi ndi akulu a Isiraeli, n’kumadzithira fumbi kumutu kwawo.+ 7 Ndipo Yoswa anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, n’chifukwa chiyani mwayendetsa anthuwa mtunda wonsewu mpaka kudzawoloka mtsinje wa Yorodano, koma n’kutipereka m’manja mwa Aamori kuti atiphe? Ndiyetu mwina zikanakhala bwino tikanaganiza zongokhala kutsidya lina lija la Yorodano!+ 8 Pepanitu Yehova, ndingatinso chiyani nanga, poona kuti Isiraeli wathawa pamaso pa adani ake? 9 Akanani ndi anthu onse a m’dziko lino adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndithu, ndi kufafaniza dzina lathu kulichotsa padziko lapansi.+ Nanga zikatero mudzaliteteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+
10 Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Dzuka iwe! N’chifukwa chiyani wadzigwetsa mpaka nkhope yako pansi? 11 Aisiraeli achimwa, ndiponso aphwanya pangano+ limene ndinawalamula kuti alisunge. Iwo atenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Aba+ zinthuzo ndi kuzibisa+ pakati pa katundu wawo.+ 12 Ana a Isiraeli sadzathanso kulimbana ndi adani awo.+ Iwo azingothawa kwa adani awo, chifukwa iwonso akhala zinthu zoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhalanso nanu kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.+ 13 Dzuka! Yeretsa anthuwa,+ uwauze kuti, ‘Mawa mudziyeretse, pakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Kalanga Isiraeli, pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Anthu inu simudzathanso kulimbana ndi adani anu, kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo. 14 Mawa m’mawa, mubwere fuko ndi fuko. Fuko limene Yehova adzasankhe+ lidzabwere patsogolo. Kenako mbumba ndi mbumba, ndipo mbumba imene Yehova adzasankhe idzabwere patsogolo. Kenako banja ndi banja, ndipo banja limene Yehova adzasankhe lidzabwere patsogolo, komanso mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha. 15 Amene apezeke ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo, adzatenthedwa ndi moto,+ iye limodzi ndi banja lake ndi zonse ali nazo. Adzatenthedwa chifukwa waphwanya pangano la Yehova,+ ndiponso wachita cholakwa chochititsa manyazi mu Isiraeli.”’”+
16 Ndiyeno Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri, n’kuuza Isiraeli kuti afike pamaso pa Mulungu, fuko ndi fuko, ndipo fuko la Yuda linasankhidwa. 17 Kenako anauza mabanja a m’fuko la Yuda kufika pamaso pa Mulungu, ndipo banja la Zera linasankhidwa. Kenako anauza banja la Zera+ kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha, ndipo Zabidi anasankhidwa. 18 Potsirizira pake anauza a m’nyumba ya Zabidi kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense wamphamvu payekhapayekha. Ndipo Akani mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anasankhidwa.+ 19 Tsopano Yoswa anauza Akani kuti: “Mwana wanga, chonde, lemekeza Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ ulula kwa iye.+ Tandiuza+ chonde, n’chiyani chimene wachita? Usandibisire.”+
20 Ndipo Akani anayankha Yoswa kuti: “Ndithu ndam’chimwira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ Zimene ndinachita ndi izi: 21 Nditaona+ chovala chamtengo wapatali cha ku Sinara,+ pakati pa katundu wotsalayo, chokongola m’maonekedwe, komanso masekeli* a siliva 200, ndi mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50, ndinazikhumba zinthuzo,+ ndipo ndinazitenga.+ Panopo chovalacho ndinachikumbira pansi, pakati pa hema wanga, pamodzi ndi ndalamazo, ndipo ndalamazo zili pansi pa chovalacho.”+
22 Nthawi yomweyo Yoswa anatuma anthu, amene anathamangira kuhemako. Iwo anachipezadi chovalacho m’hema wake, ndi ndalama zija pansi pake. 23 Anthu aja anatenga zinthuzo pakati pa hemayo, n’kubwera nazo kwa Yoswa ndi ana a Isiraeli onse, kumene anazikhuthulira pansi pamaso pa Yehova. 24 Tsopano Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ng’ombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, n’kutsikira nawo kuchigwa cha Akori.+ 25 Ndiyeno Yoswa anati: “N’chifukwa chiyani wachititsa kuti tinyanyalidwe?+ Iweyo lero Yehova akunyanyala.” Atatero, Aisiraeli onse anawaponya miyala,+ kenako anawatentha ndi moto.+ Choncho, anawaponya miyala. 26 Pambuyo pake, anaunjika mulu waukulu wa miyala pa iye. Muluwo ulipo mpaka lero.+ Zitatero, mkwiyo waukulu wa Yehova unatha.+ Ndiye chifukwa chake malowo anatchedwa chigwa cha Akori*+ mpaka lero.
8 Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Usaope kapena kuchita mantha.+ Tenga amuna onse ankhondo. Nyamuka, upite kudziko la Ai. Taona, mfumu ya Ai ndaipereka m’manja mwako limodzi ndi anthu ake, mzinda wake, ndi dziko lake.+ 2 Ukachite kwa Ai ndi mfumu yake zimene unachita kwa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto za mumzindawo mukafunkhe zikakhale zanu.+ Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”+
3 Choncho, Yoswa limodzi ndi amuna onse ankhondo+ anakonzeka kupita ku Ai. Yoswa anasankha amuna okwanira 30,000, asilikali amphamvu ndi olimba mtima,+ n’kuwatumiza usiku. 4 Anawalamula kuti: “Inu mukabisale+ kumbuyo kwa mzindawo. Musakakhale patali kwambiri ndi mzindawo, ndipo nonsenu mukakhale okonzeka. 5 Koma ine ndi onse amene akakhale ndi ine, tikafika pafupi kwambiri ndi mzindawo. Iwo akakatuluka kuti adzamenyane nafe ngati poyamba paja,+ tikathawa. 6 Akakaona choncho, akatithamangitsa. Ife tikathawa kuti tikawatulutse mpaka atafika kutali ndi mzindawo, pakuti adzati, ‘Akuthawa ngati poyamba paja.’+ 7 Zikakatero, inu mukavumbuluke ndi kukalanda mzindawo, pakuti Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu m’manja mwanu.+ 8 Ndipo mukakangoti mwalanda mzindawo, mukauyatse moto.+ Mukachite zimenezo malinga ndi mawu a Yehova. Izi n’zimene ndakulamulani.”+
9 Pambuyo pake Yoswa anawatumiza amunawo, ndipo iwo anapita kumalo okabisalako. Kumeneko anakamanga timisasa tobisalira, kumadzulo kwa Ai. Anamanga timisasato pakati pa Ai ndi Beteli. Koma usikuwo Yoswa anagona limodzi ndi asilikali amene anali nawo.
10 Kenako, Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri+ n’kuyendera asilikali ake. Atatero ananyamuka, iye limodzi ndi akulu a Isiraeli, n’kutsogolera asilikaliwo ku Ai. 11 Ankhondo onse+ amene anali limodzi ndi Yoswa anapita naye, n’kukafika pafupi ndi mzindawo kutsogolo kwake. Atafika anamanga msasa kumpoto kwa Ai, ndipo pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12 Tsopano anatenga amuna pafupifupi 5,000, nawabisa+ pakati pa Beteli+ ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda wa Ai. 13 Choncho asilikaliwo anakhazikitsa msasa wawo waukulu kumpoto kwa mzindawo,+ ndipo wina anaukhazikitsa kumadzulo,+ kumbuyo kwenikweni kwa mzindawo. Usikuwo Yoswa ananyamuka n’kupita pakati pa chigwacho.
14 Tsopano mfumu ya Ai itangoona zimenezo, amuna a mumzindawo anakonzekera msangamsanga. M’mawa mwake analawirira kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Mfumuyo limodzi ndi anthu ake onse, ananyamuka pa nthawi imene anapangana, ndipo analowera kuchigwa cha m’chipululu. Koma mfumuyo sinadziwe kuti asilikali ena anali atabisala kumbuyo kwa mzindawo.+ 15 Pofuna kuonetsa ngati akugonja, Yoswa limodzi ndi Aisiraeli onse amene anali naye+ anathawa kudzera njira yolowera kuchipululu.+ 16 Zitatero, anthu onse a mumzindawo anaitanidwa kuti akathamangitse Aisiraeli. Anthuwo anathamangitsa Aisiraeliwo limodzi ndi Yoswa, mpaka anafika kutali ndi mzinda wawo.+ 17 Panalibe mwamuna ndi mmodzi yemwe amene anatsala mu Ai ndi m’Beteli. Onse anapita kukathamangitsa Aisiraeli, moti zipata za mzindawo anangozisiya zosatseka.
18 Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Lozetsa nthungo* imene ili m’dzanja lako ku Ai,+ pakuti mzindawo ndaupereka m’manja mwako.”+ Chotero Yoswa analozetsa kumzindawo nthungo imene inali m’dzanja lake. 19 Pamenepo, asilikali amene anabisala aja anavumbuluka pamalo pamene anali. Pa nthawi imene iye anatambasula dzanja lake, iwo anathamanga n’kukalowa mumzindawo n’kuulanda.+ Atatero, anauyatsa moto mzindawo mofulumira.+
20 Amuna a ku Ai atacheuka anangoona utsi uli tolo mumzindawo, ndipo anasoweratu mphamvu zoti n’kuthawira kwina kulikonse. Pamenepo asilikali achiisiraeli amene ankathawira kuchipululu aja, anatembenukira amuna a ku Aiwo. 21 Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye ataona kuti asilikali omwe anabisala+ aja alanda mzindawo, ndiponso utsi ukufuka mumzindawo, anatembenukira amuna a ku Ai n’kuyamba kuwapha. 22 Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Chotero amuna a ku Ai anakhala pakati pa Aisiraeli, ena mbali iyi, ena mbali inayo. Pamenepo Aisiraeli anapha amuna a ku Ai, moti panalibe wotsala ndi moyo kapena wothawa.+ 23 Koma mfumu+ ya Ai anaigwira, n’kubwera nayo yamoyo kwa Yoswa.
24 Aisiraeli anapitiriza kupha amuna ankhondo onse a ku Ai. Anawaphera kuchipululu kumene anthu a ku Aiwo anathamangitsirako Aisiraeli. Anawapha ndi lupanga mpaka kuwatha onse. Atatero, Aisiraeliwo anabwerera ku Ai, n’kukapha ndi lupanga ena onse otsala. 25 Anthu onse amene anaphedwa tsikulo, amuna ndi akazi, anakwana 12,000, anthu onse a ku Ai. 26 Ndipo Yoswa sanatsitse mkono wake umene anautambasula polozetsa nthungo+ kumzindawo, mpaka anthu onse a ku Ai ataphedwa.+ 27 Koma Aisiraeliwo anafunkha ziweto ndi katundu wa mumzindawo n’kukhala zawo, malinga ndi zimene Yehova analamula Yoswa.+
28 Chotero Yoswa anatentha mzinda wa Ai+ n’kuusiya uli bwinja lokhalapo mpaka kalekale, ndipo lilipobe mpaka lero. 29 Ndipo mfumu ya Ai+ anaipachika pamtengo mpaka madzulo.+ Koma dzuwa litatsala pang’ono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo+ pamtengopo. Atauchotsa mtembowo anakauponya pachipata cha mzindawo, n’kuufotsera ndi mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero.
30 Inali nthawi imeneyi pamene Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Isiraeli guwa lansembe+ m’phiri la Ebala.+ 31 Anamanga guwalo mogwirizana ndi zimene Mose mtumiki wa Yehova analamula ana a Isiraeli, monga mwa zolembedwa m’buku la chilamulo+ cha Mose, zimene zimati: “Guwa lansembe la miyala yathunthu, yosasema ndi chipangizo chachitsulo.”+ Ndipo iwo anaperekerapo kwa Yehova nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.+
32 Kenako, Yoswa analemba pamiyala+ chilamulo chimene Mose analembera ana a Isiraeli.+ 33 Aisiraeli onse, atsogoleri awo,+ akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo okhala pakati pawo.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa ansembe+ achilevi. Ansembewo anali atanyamula likasa la pangano la Yehova.+ Hafu ya anthuwo inaima m’phiri la Gerizimu,+ ndipo hafu ina inaima m’phiri la Ebala,+ (monga mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira,)+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe+ choyamba. 34 Pambuyo pake, Yoswa anawerenga mokweza mawu onse a chilamulo,+ madalitso+ ndi matemberero,+ malinga ndi zonse zolembedwa m’buku la chilamulo. 35 Panalibe ngakhale liwu limodzi pamawu onse amene Mose analamula, limene Yoswa sanaliwerenge mokweza pamaso pa mpingo wonse wa Aisiraeli.+ Akazi+ ndi ana aang’ono,+ komanso alendo okhala pakati pawo+ anali pomwepo.
9 Mafumu+ a kutsidya kwa Yorodano anamva zimene zinachitika. Amenewa anali mafumu a Ahiti,+ Aamori, Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi ndi Ayebusi.+ Iwo anali kukhala kudera lamapiri, ndiponso ku Sefela, ndi m’mbali monse mwa Nyanja Yaikulu,+ komanso pafupi ndi Lebanoni.+ Mafumu onsewo atangomva zimene zinachitikazo, 2 anasonkhanitsa pamodzi magulu awo ankhondo kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.+
3 Anthu a ku Gibeoni+ anamva zimene Yoswa anachita ku Yeriko+ ndi Ai.+ 4 Atamva choncho, paokha anachitapo kanthu mwanzeru.+ Ananyamula chakudya m’matumba akutha n’kukweza pa abulu awo. Ananyamulanso vinyo m’matumba achikopa akutha, omangamanga mong’ambika.+ 5 Anavala nsapato zakutha zosokererasokerera, ndi zovala zansanza. Mkate wawo wonse wa kamba wa pa ulendo unali wouma ndi wofumbutuka. 6 Kenako anapita kwa Yoswa kumsasa wa ku Giligala,+ ndipo anauza iye ndi amuna achiisiraeli kuti: “Ife tachokera kudziko lakutali kwambiri. Chonde, chitani nafe pangano.”+ 7 Koma amuna achiisiraeli anayankha Ahiviwo+ kuti: “Mwinamwake mumakhala pafupi chakonkuno. Ndiye tingachite nanu bwanji pangano?”+ 8 Iwo poyankha anauza Yoswa kuti: “Ndife okonzeka kukhala akapolo anu.”+
Ndiyeno Yoswa anawafunsanso kuti: “Koma ndinu ndani makamaka, ndipo mwachokera kuti?” 9 Iwo anamuyankha kuti: “Akapolo anufe tachokera kudziko lakutali kwambiri.+ Tabwera chifukwa tamva za dzina+ la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita ku Iguputo.+ 10 Tamvanso zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kutsidya lina la Yorodano. Mafumuwo ndiwo Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali ku Asitaroti.+ 11 Pakumva zimenezi, akulu akwathu ndi anthu onse a m’dziko lathu anatiuza kuti,+ ‘Tengani kamba wa pa ulendo, mupite mukakumane nawo. Mukawauze kuti: “Ife ndife akapolo anu.+ Chonde chitani nafe pangano.”’+ 12 Tsiku limene tinanyamuka kunyumba kubwera kwa inu, mkate wathuwu umene tinautenga monga kamba wa pa ulendo unali wotentha. Koma taonani! Tsopano wauma ndipo ukufumbutuka.+ 13 Taonaninso matumba achikopa a vinyowa. Matumba amenewa anali atsopano pamene timathiramo vinyo, koma tsopano atha ndi kung’ambika.+ Komanso onani zovala zathu ndi nsapato zathuzi, zang’ambika chifukwa cha kutalika kwa ulendo.”
14 Pamenepo amuna achiisiraeli anatengako zakudyazo kuti aziyang’anitsitse, ndipo sanafunsire kwa Yehova.+ 15 Choncho Yoswa anagwirizana nawo za mtendere,+ ndipo anachita nawo pangano kuti asawaphe. Zitatero, atsogoleri+ a Isiraeli analumbira kwa anthuwo.+
16 Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo anali apafupi, ndi kuti anali kukhala m’dera lomwelo. 17 Pamenepo Aisiraeliwo ananyamuka n’kukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibeoni,+ Kefira,+ Beeroti,+ ndi Kiriyati-yearimu.+ 18 Ana a Isiraeli sanawaphe anthuwo. Sanawaphe chifukwa atsogoleri a khamu la ana a Isiraeli anali atalumbirira+ anthuwo pali Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ Choncho, khamu lonse linayamba kung’ung’udza motsutsana ndi atsogoleriwo.+ 19 Pamenepo atsogoleri onse anauza khamu lonselo kuti: “Ife tinawalumbirira pali Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndipo tsopano sitingawachitire choipa.+ 20 Tiwasiya kuti akhale ndi moyo, kuti Mulungu asatikwiyire chifukwa cha lumbiro limene tinawalumbirira.”+ 21 Ndiyeno atsogoleriwo anawauza kuti: “Akhale ndi moyo, ndipo akhale otola nkhuni ndi otungira madzi khamu lonse la Isiraeli,+ monga mmene tinawalonjezera.”+
22 Pambuyo pake Yoswa anaitana anthuwo, n’kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani munatipusitsa ponena kuti ‘Timakhala kutali kwambiri ndi inu,’+ pamene mukukhala nafe pafupi chonchi?+ 23 Tsopano mukhala anthu otembereredwa.+ Mukhala akapolo+ otola nkhuni ndi otungira madzi nyumba ya Mulungu wanga ku nthawi yonse.”+ 24 Anthuwo anamuyankha Yoswa kuti: “Akapolo anufe tinachita zimenezi+ chifukwa tinali ndi mantha aakulu.+ Tinachita mantha titauzidwa mosapita m’mbali za Yehova Mulungu wanu. Tinamva kuti analamula mtumiki wake Mose kuti akupatseni dziko lonse lino, ndi kuti muphe anthu onse okhalamo.+ 25 Tsopano tadzipereka m’manja mwanu. Muchite nafe chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino ndi choyenera kwa inu.”+ 26 Yoswa anavomereza kuchita nawo motero. Anawalanditsa kwa ana a Isiraeli kuti asawaphe.+ 27 Chotero pa tsikuli, Yoswa anawaika+ kukhala otola nkhuni ndi otungira madzi Aisiraeli,+ ndiponso kuti azitola nkhuni ndi kutunga madzi a paguwa lansembe la Yehova, pamalo alionse amene Mulungu wasankha.+ Iwo akhala akuchita zimenezi mpaka lero.
10 Tsopano Adoni-zedeki, mfumu ya Yerusalemu anamva zakuti Yoswa walanda mzinda wa Ai+ ndi kuuwononga.+ Iye anamva kuti Yoswa wawononga mzindawo ndi kupha mfumu yake+ monga anachitira ndi mzinda wa Yeriko+ ndi mfumu yake.+ Anamvanso kuti anthu okhala ku Gibeoni apangana za mtendere ndi Aisiraeli+ ndipo akukhala pakati pawo. Atangomva zimenezi, 2 Adoni-zedeki anachita mantha kwambiri+ chifukwa Gibeoni unali mzinda waukulu ngati mzinda wolamulidwa ndi mfumu. Komanso mzindawo unali waukulu kuposa mzinda wa Ai,+ ndiponso amuna onse a kumeneko anali amphamvu. 3 Pamenepo Adoni-zedeki mfumu ya Yerusalemu+ anatumiza uthenga kwa Hohamu mfumu ya ku Heburoni,+ kwa Piramu mfumu ya ku Yarimuti,+ kwa Yafiya mfumu ya ku Lakisi+ ndi kwa Debiri mfumu ya ku Egiloni.+ Anatumiza uthenga wakuti: 4 “Bwerani kuno mudzandithandize. Tiyeni tikakanthe Agibeoni, chifukwa apangana za mtendere ndi Yoswa ndi ana a Isiraeli.”+ 5 Choncho mafumu asanu a Aamoriwo+ anakumana pamodzi n’kunyamuka. Mafumuwo anali: Mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni. Mafumu amenewa, pamodzi ndi magulu awo ankhondo anakamanga msasa pafupi ndi mzinda wa Gibeoni, n’cholinga chouthira nkhondo.
6 Amuna a ku Gibeoni ataona zimenezi, anatumiza uthenga kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ kuti: “Musatitaye ife akapolo anu!+ Bwerani kuno msanga, mudzatithandize ndi kutipulumutsa. Mafumu onse a Aamori okhala kudera lamapiri atisonkhanira kuti atithire nkhondo.” 7 Chotero Yoswa limodzi ndi amuna onse ankhondo, ndiponso amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ ananyamuka kuchokera ku Giligala.+
8 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa ndawapereka m’manja mwako.+ Palibe aliyense amene adzatha kulimbana nawe.”+ 9 Yoswa anayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, ndipo anatulukira adaniwo modzidzimutsa. 10 Pamenepo Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndiyeno Aisiraeli anayamba kupha adaniwo kwadzaoneni ku Gibeoni,+ ndi kuwathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni. Ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka+ ndi ku Makeda.+ 11 Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anawagwetsera miyala ikuluikulu ya matalala+ kuchokera kumwamba yomwe inawagwera ndi kuwapha mpaka kukafika ku Azeka. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene ana a Isiraeli anapha ndi lupanga.
12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori kwa ana a Isiraeli, Yoswa analankhula ndi Yehova pamaso pa Aisiraeli kuti:
“Dzuwa iwe,+ ima pamwamba pa Gibeoni,+
Ndipo iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Aijaloni.”+
13 Choncho dzuwa linaimadi, ndiponso mwezi unaima mpaka mtunduwo utalanga adani ake.+ Kodi sizinalembedwe m’buku la Yasari?+ Dzuwa linaima kumwamba pakatikati, silinafulumire kulowa pafupifupi kwa tsiku lonse lathunthu.+ 14 Palibe tsiku lina lofanana ndi limenelo, kaya pambuyo pake kapena patsogolo pake, loti Yehova anamvera mawu a munthu mwa njira imeneyi,+ popeza Yehova mwiniyo anali kumenyera nkhondo Isiraeli.+
15 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anabwerera kumsasa ku Giligala.+
16 Koma mafumu asanu aja anathawa+ n’kukabisala kuphanga la ku Makeda.+ 17 Ndiyeno Yoswa analandira uthenga wakuti: “Mafumu asanu aja apezeka atabisala kuphanga la ku Makeda.”+ 18 Yoswa atamva anati: “Gubuduzirani miyala ikuluikulu pakamwa pa phangalo ndipo musankhe amuna oti azilonderapo. 19 Koma amuna enanu, musangoima chilili. Thamangitsani adani anu ndipo muzipha amene muziwapeza.+ Musawalole kuti akalowe m’mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka m’manja mwanu.”+
20 Yoswa ndi ana a Isiraeli atangomaliza kupulula adani awo onse,+ ndipo opulumuka atathawa n’kukalowa m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ 21 Aisiraeli onse anayamba kubwerera mwamtendere kwa Yoswa kumsasa, ku Makeda. Ndipo palibe munthu amene ananena zamtopola kwa ana a Isiraeli.+ 22 Ndiyeno Yoswa anati: “Tsegulani phangali munditulutsire mafumu asanu amene ali mmenemowo.” 23 Iwo anatseguladi phangalo n’kumutulutsira mafumu asanuwo: Mfumu ya ku Yerusalemu,+ mfumu ya ku Heburoni,+ mfumu ya ku Yarimuti,+ mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.+ 24 Atangowatulutsa mafumuwo anapita nawo kwa Yoswa. Iye anaitana amuna onse a Isiraeli amene anapita naye kunkhondoko, n’kuuza atsogoleri awo kuti: “Bwerani kuno muponde kumbuyo kwa makosi a mafumuwa.”+ Iwo anabwera n’kupondadi kumbuyo kwa makosi awo.+ 25 Ndiyeno Yoswa anawauza kuti: “Musaope kapena kuchita mantha.+ Khalani olimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu, chifukwa umu ndi mmene Yehova azichitira ndi adani anu onse amene mukumenyana nawo.”+
26 Kenako Yoswa anawakantha ndi kuwapha. Atatero anawapachika pamitengo isanu, pomwe anakhalapo mpaka madzulo.+ 27 Dzuwa likulowa, Yoswa analamula kuti atsitse mafumuwo pamitengoyo+ n’kuwaponyera m’phanga limene anabisalamo lija, ndipo anthuwo anachitadi zimenezi. Kenako anaika miyala ikuluikulu pakhomo la phangalo, yomwe ilipobe mpaka lero.
28 Yoswa analanda mzinda wa Makeda+ tsiku limenelo ndipo anapha anthu a mumzindawo ndi lupanga. Mfumu ya mzindawo ndi anthu ake onse anawapha,+ ndipo Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Makeda+ anaichita zofanana ndi zomwe anachita mfumu ya ku Yeriko.
29 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Makeda n’kupita ku Libina+ komwe anakachitako nkhondo. 30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake m’manja mwa Isiraeli. Choncho Aisiraeli anapha anthu onse a mumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anachita mfumu ya ku Yeriko.+
31 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse omwe anali naye anachoka ku Libina n’kupita ku Lakisi.+ Kumeneko anamanga msasa pafupi ndi mzindawo n’kuuthira nkhondo. 32 Yehova anapereka Lakisi m’manja mwa Isiraeli, moti analanda mzindawo pa tsiku lachiwiri. Anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo,+ mofanana ndi zonse zimene anachita ku Libina.
33 Apa m’pamene Horamu mfumu ya ku Gezeri+ anapita kukathandiza mzinda wa Lakisi. Koma Yoswa anapha Horamu ndi anthu ake onse, moti sipanatsale wopulumuka.+
34 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Lakisi n’kupita ku Egiloni.+ Kumeneko anakamanga msasa pafupi ndi mzindawo n’kuuthira nkhondo. 35 Analanda mzindawo pa tsikulo n’kuyamba kupha ndi lupanga aliyense amene anali mumzindawo. Anachitira mzindawo zonse zimene anachitira mzinda wa Lakisi.+
36 Atachoka ku Egiloni, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anapita kumzinda wa Heburoni+ n’kuyamba kuuthira nkhondo. 37 Analanda mzindawo ndipo anapha ndi lupanga anthu amene anali mmenemo ndi m’midzi yake yonse, komanso anapha mfumu yawo. Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Anachitira mzindawo zonse zimene anachitira mzinda wa Egiloni. Chotero Yoswa anawononga mzindawo ndi aliyense amene anali mmenemo.+
38 Pomaliza, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye, anatembenuka n’kupita kumzinda wa Debiri,+ n’kuyamba kuuthira nkhondo. 39 Analanda mzindawo ndi midzi yake yonse n’kugwiranso mfumu yake. Ndiyeno anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mmenemo,+ ndipo Yoswa anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Anachitira mzinda wa Debiri ndi mfumu yake zonse zimene anachitira mzinda wa Heburoni, komanso zimene anachitira mzinda wa Libina ndi mfumu yake.+
40 Choncho Yoswa anapha anthu a m’dera lonse la mapiri,+ anthu a ku Negebu,+ a ku Sefela,+ ndi a m’madera otsetsereka+ pamodzi ndi mafumu awo onse. Iye anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka,+ ndipo anapha chamoyo chilichonse*+ monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamulira.+ 41 Yoswa anawapha kuchokera ku Kadesi-barinea+ mpaka ku Gaza+ ndi dera lonse la Goseni+ mpaka ku Gibeoni.+ 42 Yoswa anagwira mafumu onsewa n’kulanda malo awo pa nthawi imodzi,+ chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndiye anali kuwamenyera nkhondo.+ 43 Atatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anabwerera kumsasa ku Giligala.+
11 Ndiyeno Yabini mfumu ya ku Hazori+ atangomva nkhaniyi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni, ndi mfumu ya ku Simironi, ndiponso mfumu ya ku Akasafu.+ 2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amene anali m’dera lamapiri kumpoto, ndiponso m’chipululu kum’mwera kwa nyanja ya Kinereti,*+ mafumu a ku Sefela,+ ndiponso kwa mafumu okhala m’mapiri a Dori+ kumadzulo. 3 Anaitanitsanso Akanani+ okhala kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso Aamori,+ Ahiti,+ Aperezi+ ndi Ayebusi+ okhala kudera lamapiri. Komanso anaitanitsa Ahivi+ omwe anali kukhala m’munsi mwa phiri la Herimoni+ ku Mizipa.+ 4 Choncho mafumuwo pamodzi ndi magulu awo onse ankhondo ananyamuka. Anali anthu ambiri, kuchuluka kwawo ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo anali ndi mahatchi*+ ambiri zedi komanso magaleta* ankhondo. 5 Mafumu onsewa anakumana pamodzi monga anapanganirana. Ndiyeno onse pamodzi anakamanga msasa pafupi ndi madzi a ku Meromu kuti akamenyane ndi Aisiraeli.+
6 Pamenepo Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ pakuti mawa pa nthawi ngati yomwe ino, ndidzawapereka onsewo kuti aphedwe ndi Aisiraeli. Mahatchi awo udzawapundula,*+ ndipo magaleta awo udzawatentha ndi moto.”+ 7 Yoswa ndi asilikali ake onse anapita kufupi ndi madzi a Meromu ndi kuthira nkhondo adaniwo modzidzimutsa. 8 Ndipo Yehova anapereka adaniwo m’manja mwa Aisiraeli.+ Chotero anayamba kuwapha ndi kuwathamangitsa mpaka kukafika kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe+ kum’mawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+ 9 Pambuyo pake Yoswa anachita zimene Yehova anamuuza. Mahatchi awo anawapundula,+ ndipo magaleta awo anawatentha ndi moto.+
10 Kuwonjezera apo, Yoswa anabwerera ndi kukalanda+ mzinda wa Hazori+ n’kupha mfumu yake ndi lupanga.+ Anachita zimenezi chifukwa mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa. 11 Aisiraeliwo anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo.+ Panalibe chamoyo chilichonse chimene chinatsala,+ ndipo Yoswa anatentha mzinda wa Hazori ndi moto. 12 Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, ndi kugwira mafumu onse a mizindayi n’kuwapha ndi lupanga.+ Anawawononga onsewo+ monga mmene analamulira Mose mtumiki wa Yehova.+ 13 Mizinda yonse imene inamangidwa pamabwinja a mizinda yakale, Aisiraeli sanaitenthe ndi moto, kupatulapo mzinda wa Hazori umene Yoswa anautentha ndi moto. 14 Ana a Isiraeli anafunkha katundu yense wa m’mizindayi ndi ziweto zomwe.+ Koma anthu anawapha ndi lupanga kufikira atawamaliza onse.+ Sanasiye munthu aliyense wamoyo.+ 15 Monga Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamula Yoswa,+ ndipo Yoswayo anachitadi zimenezo. Palibe mawu alionse amene Yoswa anasiya pa mawu onse amene Yehova analamula Mose.+
16 Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni,+ ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake.+ 17 Analandanso dera lochokera kuphiri la Halaki+ lomwe lili moyang’anizana ndi Seiri+ mpaka kukafika ku Baala-gadi,+ kuchigwa cha Lebanoni m’munsi mwa phiri la Herimoni.+ Yoswa anagwira mafumu awo onse ndi kuwapha.+ 18 Iye anachita nkhondo ndi mafumu onsewa kwa masiku ambiri. 19 Panalibe mzinda winanso umene unapangana za mtendere ndi ana a Isiraeli kupatulapo Ahivi+ okhala mumzinda wa Gibeoni.+ Ana a Isiraeli analanda mizinda ina yonse mwankhondo.+ 20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+
21 Kuwonjezera apo, pa nthawiyo Yoswa anapita n’kukafafaniziratu Aanaki.+ Aanakiwo anali kukhala kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi,+ kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli.+ Yoswa anafafaniziratu Aanakiwo pamodzi ndi mizinda yawo.+ 22 M’dziko la ana a Isiraeli, palibe Aanaki amene anatsalamo,+ kupatulapo okhala ku Gaza,+ ku Gati+ ndi ku Asidodi.+ 23 Chotero Yoswa analanda dziko lonse monga mmene Yehova analonjezera Mose.+ Ndiyeno Yoswa anapereka dzikolo kwa Aisiraeli monga cholowa chawo, malinga ndi magawo awo potsata mafuko awo.+ Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+
12 Tsopano awa ndi mafumu amene ana a Isiraeli anagonjetsa n’kulanda madera awo, kumbali yotulukira dzuwa+ ya mtsinje wa Yorodano. Analanda kuchokera kuchigwa* cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba+ konse, kumbali yotulukira dzuwa. Mafumu ake ndi awa: 2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni.+ Dera lomwe anali kulamulira linkayambira pakatikati pa chigwa cha Arinoni kuphatikizapo mzinda wa Aroweli,+ umene unali m’mphepete mwa mtsinje wa Arinoni,+ mpaka hafu ya Giliyadi kukalekezera kuchigwa cha Yaboki,+ kumalire ndi ana a Amoni. 3 Anali kulamuliranso chigwa cha Araba+ mpaka kunyanja ya Kinereti+ kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, n’kukafikanso kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.+ Anali kulamulira kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, cha ku Beti-yesimoti,+ mpaka kum’mwera, kumunsi kwa Pisiga.+
4 Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi mwa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti+ ndi ku Edirei.+ 5 Anali kulamulira kuphiri la Herimoni,+ ku Saleka, ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri+ ndi Amaakati.+ Anali kulamuliranso hafu ya Giliyadi, mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni,+ mfumu ya Hesiboni,+ anali kulamulira.
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Isiraeli ndiwo anagonjetsa mafumuwa.+ Atatero, Mose mtumiki wa Yehova anapereka dzikoli kwa Arubeni,+ Agadi,+ ndi hafu ya fuko la Manase,+ kuti likhale lawo.
7 Yoswa ndi ana a Isiraeli anagonjetsa mafumu a kudera la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyang’anizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa m’magawomagawo.+ 8 Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu, ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:
9 Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi.
10 Mfumu ya Yerusalemu,+ imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi.
11 Mfumu ya Yarimuti,+ imodzi. Mfumu ya Lakisi,+ imodzi.
12 Mfumu ya Egiloni,+ imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi.
13 Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi.
14 Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi.
15 Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi.
16 Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi.
17 Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi,+ imodzi.
18 Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi.
19 Mfumu ya Madoni,+ imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi.
20 Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu,+ imodzi.
21 Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido,+ imodzi.
22 Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi.
23 Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi.
13 Tsopano Yoswa anali atakalamba, ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Choncho Yehova anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba ndipo uli ndi zaka zambiri, koma dziko loti lilandidwe likadali lalikulu.+ 2 Dziko limene latsala ndi ili:+ Madera onse a Afilisiti+ ndi madera onse a Agesuri.+ 3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo kum’mawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi,+ ankalitcha dziko la Akanani.)+ Madera a Afilisitiwa akulamulidwa ndi olamulira ogwirizana asanu.+ Maderawo ndi Gaza,+ Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ komanso Aavi+ akukhala komweko. 4 Kum’mwera kwatsala dziko lonse la Akanani. Patsalanso mzinda wa Asidoni+ wotchedwa Meara, mpaka kukafika ku Afeki kumalire a Aamori, 5 dziko la Agebala+ ndiponso dziko lonse la Lebanoni, kotulukira dzuwa, kuyambira ku Baala-gadi+ m’munsi mwa phiri la Herimoni mpaka kumalire ndi Hamati.+ 6 Ine ndidzapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu,+ ndidzapitikitsa Asidoni onse.+ Iweyo ungopereka dzikoli kwa ana a Isiraeli+ kuti likhale cholowa chawo monga mmene ndinakulamulira.+ 7 Dzikoli uligawe kwa mafuko 9 ndiponso kwa hafu ya fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”+
8 Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa Arubeni ndi kwa Agadi, kutsidya la kum’mawa kwa Yorodano.+ 9 Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwererapo a Medeba+ mpaka kukafika ku Diboni.+ 10 Anawapatsanso mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ku Hesiboni, mpaka kumalire ndi ana a Amoni.+ 11 Anapatsidwanso dera la Giliyadi, la Agesuri,+ la Amaakati, phiri lonse la Herimoni,+ ndi dera lonse la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12 Mafukowa anatenganso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei.+ Mfumu Ogi anali mmodzi mwa Arefai otsala.+ Mose anagonjetsa anthu onsewa ndi kuwapitikitsa.+ 13 Koma ana a Isiraeli sanapitikitse+ Agesuri ndi Amaakati. Ndipo iwo+ akukhalabe pakati pawo kufikira lero.
14 Fuko la Alevi lokha ndi limene sanalipatse cholowa cha malo.+ Cholowa chawo ndicho nsembe zotentha ndi moto+ zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga mmene anawalonjezera.+
15 Tsopano Mose anagawira dziko ana a Rubeni potsata mabanja awo. 16 Dziko lawo linayambira ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikoli linaphatikizapo malo onse okwererapo apafupi ndi Medeba,+ 17 Hesiboni,+ ndi midzi yake yonse+ imene inali m’malo okwererapowo. Linaphatikizaponso Diboni,+ Bamoti-baala,+ Beti-baala-meoni,+ 18 Yahazi,+ Kademoti,+ Mefaata,+ 19 Kiriyataimu,+ Sibima,+ Zereti-sahara, malo amene anali m’phiri la kuchigwa, 20 Beti-peori, dera lotsetsereka la ku Pisiga,+ Beti-yesimoti,+ 21 mizinda yonse ya m’malo okwererapo,+ ndiponso dziko lonse la Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ili ku Hesiboni.+ Mfumu imeneyi Mose anaipha+ limodzi ndi atsogoleri a ku Midiyani, Evi, Rekemu, Zuri, Hura, ndi Reba.+ Amenewa anali mafumu omwe anali pansi pa Sihoni ndipo anali kukhala m’dzikolo. 22 Pakati pa anthu amene ana a Isiraeli anawapha ndi lupanga, panali Balamu mwana wa Beori,+ wolosera zam’tsogolo+ uja. 23 Malire a ana a Rubeni anali mtsinje wa Yorodano. Limeneli ndilo gawo la ana a Rubeni+ limene anapatsidwa potsata mabanja awo. Iwo anapatsidwa mizinda ndi midzi ya kumeneko kuti ikhale cholowa chawo.
24 Kenako Mose anagawira dziko fuko la ana a Gadi potsata mabanja awo.+ 25 Gawo lawo linayambira kumzinda wa Yazeri,+ mizinda yonse ya ku Giliyadi,+ ndi hafu ya dziko la ana a Amoni,+ mpaka kukafika ku Aroweli+ kufupi ndi Raba.+ 26 Kuchokera ku Hesiboni+ linakafika ku Ramati-mizipe ndi ku Betonimu, ndiponso kuchokera ku Mahanaimu+ mpaka kumalire ndi Debiri.+ 27 Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya m’chigwa ya Beti-harana,+ Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni, ndi mbali yotsala ya dziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndiwo unali malire awo mpaka kunyanja ya Kinereti.+ Gawo lawo linali kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28 Ili ndilo dziko limene ana a Gadi+ anapatsidwa monga cholowa chawo potsata mabanja awo. Anapatsidwa mizinda ya kumeneko ndi midzi yake yomwe.
29 Kenako Mose anapereka dziko kwa hafu ya fuko la Manase potsata mabanja awo, ndipo dzikolo linakhala la ana a Manase.+ 30 Gawo lawo linayambira ku Mahanaimu+ kuphatikizapo dera lonse la Basana,+ ndi dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, ndiponso midzi yonse ing’onoing’ono ya Yairi+ ku Basana. Gawo lawoli linali ndi matauni 60 onse pamodzi. 31 Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti,+ Edirei,+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi m’dziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri potsata mabanja awo.
32 Limeneli ndilo dziko limene Mose anawapatsa kuti likhale cholowa chawo, pamene anali ku Yeriko, kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano m’chipululu cha Mowabu, kum’mawa.+
33 Fuko la Alevi, Mose sanalipatse cholowa cha malo.+ Yehova Mulungu wa Isiraeli ndiye cholowa chawo, monga mmene anawalonjezera.+
14 Limeneli ndilo dziko limene ana a Isiraeli anatenga monga cholowa chawo m’dziko la Kanani.+ Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a makolo a ana a Isiraeli, ndiwo anagawa dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+ 2 Anagawira cholowacho mafuko 9 ndi hafu, mwa kuchita maere,+ monga mmene Yehova analamulira kudzera mwa Mose.+ 3 Mose anali atagawira kale cholowa mafuko awiri ndi hafu kutsidya lina la Yorodano.+ Koma Alevi sanawapatse cholowa pakati pawo.+ 4 Ana a Yosefe anakhala mafuko awiri,+ la Manase+ ndi la Efuraimu.+ Iwowa anapatsa Alevi mizinda+ yoti azikhalamo, malo odyetserako ziweto, ndi osungirako katundu wawo, koma sanawagawire cholowa cha malo.+ 5 Ana a Isiraeli anagawadi dzikolo monga mmene Yehova analamulira Mose.
6 Tsopano ana a Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi,+ anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino za mawu amene Yehova analankhula+ kwa Mose munthu wa Mulungu woona,+ onena za ine ndi inu ku Kadesi-barinea.+ 7 Ndinali ndi zaka 40 pamene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kukazonda dziko,+ kuchokera ku Kadesi-barinea. Nditabwerako ndinamuuza kuchokera pansi pa mtima wanga, zonse zimene ndinaona.+ 8 Anthu amene ndinapita nawo, anapangitsa mitima ya anthu kuchita mantha kwambiri.+ Koma ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.+ 9 Chotero Mose anandilumbirira tsiku limenelo kuti, ‘Dziko limene wakaliponda ndi mapazi ako+ lidzakhala cholowa chako ndi cha ana ako mpaka kalekale, chifukwa watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’+ 10 Yehova wandisunga ndi moyo+ monga mmene analonjezera.+ Tsopano padutsa zaka 45 kuchokera pamene Yehova analonjeza Mose, pa nthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu,+ ndipo lero ndili ndi zaka 85. 11 Komabe ndikadali ndi mphamvu monga ndinalili pa tsiku limene Mose anandituma.+ Mmene mphamvu zanga zinalili pa nthawiyo, ndi mmenenso zilili panopa, moti ndikhoza kupita kunkhondo ndi kubwerako.+ 12 Choncho, ndipatseni dera lamapiri ili limene Yehova anandilonjeza pa tsiku lija.+ Pa tsikulo, ngakhale inuyo munamva kuti kumeneko kuli Aanaki+ ndi mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma mosakayikira Yehova akakhala nane,+ ndipo ndikawapitikitsa ndithu monga mmene Yehova analonjezera.”+
13 Pamenepo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune, ndi kum’patsa mzinda wa Heburoni monga cholowa chake.+ 14 N’chifukwa chake mzinda wa Heburoni uli cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, kufikira lero. Anam’patsa mzindawo chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ 15 Zimenezi zisanachitike, mzinda wa Heburoni unkatchedwa Kiriyati-ariba+ (Ariba+ anali munthu wamphamvu pakati pa Aanaki). Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+
15 Gawo+ la fuko la ana a Yuda potsata mabanja awo linkafika kumalire a Edomu,+ ndi kuchipululu cha Zini,+ mpaka kothera kwa Negebu,+ kum’mwera. 2 Malire awo a kum’mwera ankayambira kumapeto kwa Nyanja Yamchere,+ kugombe lake la kum’mwera. 3 Malirewo analowera kum’mwera kuchitunda cha Akirabimu+ n’kukafika ku Zini.+ Kenako anakwera kuchokera kum’mwera kupita ku Kadesi-barinea,+ n’kukadutsa ku Hezironi mpaka ku Adara, n’kuzungulira kukafika ku Karika. 4 Ndiyeno anapitirira kukafika ku Azimoni+ mpaka kuchigwa cha Iguputo,+ n’kukathera kunyanja. Amenewa ndiwo anali malire awo a kum’mwera.
5 Malire a kum’mawa anali Nyanja Yamchere mpaka pamene mtsinje wa Yorodano umathirira m’nyanjayi. Malire a gawoli kumpoto, anakhota pagombe pamene mtsinje wa Yorodano umathirira m’nyanjayi.+ 6 Malirewo anapitirira mpaka ku Beti-hogila+ n’kukadutsa kumpoto kwa Beti-araba,+ n’kukafika kumwala wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 7 Anakafika ku Debiri kuchigwa cha Akori+ n’kukhotera kumpoto cha ku Giligala,+ patsogolo pa chitunda cha Adumi, kum’mwera kwa chigwa cha mtsinje. Malirewo anapitirira n’kukafika kumadzi a Eni-semesi,+ n’kukathera ku Eni-rogeli.+ 8 Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kum’mwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyang’anizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai,+ kumapeto kwa chigwacho. 9 Kuchokera pamwamba pa phirilo, malirewo anakafika kukasupe wa madzi a Nafitoa,+ n’kupitirira mpaka kumizinda ya m’mphepete mwa phiri la Efuroni. Anapitirirabe mpaka ku Baala,+ kutanthauza Kiriyati-yearimu.+ 10 Kuchokera ku Baala, malirewo anazungulira chakumadzulo kulowera kuphiri la Seiri, n’kukadutsa pamalo otsetsereka a phiri la Yearimu kumpoto, kutanthauza Kesaloni. Ndiyeno anatsetserekera ku Beti-semesi,+ n’kukafika ku Timuna.+ 11 Malirewo anakafika kumalo otsetsereka otchedwa Ekironi+ kumpoto, n’kukadutsa ku Sikeroni. Anapitirira mpaka kuphiri la Baala kukafika ku Yabineeli, n’kukathera kunyanja.
12 Malire a kumadzulo anali Nyanja Yaikulu+ ndi gombe lake. Amenewa ndiwo anali malire onse a ana a Yuda potsata mabanja awo.
13 Kalebe+ mwana wa Yefune anam’patsa gawo lake pakati pa ana a Yuda pomvera lamulo la Yehova kwa Yoswa. Anam’patsa Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali tate wa Anaki.) 14 Choncho Kalebe anapitikitsa ana atatu a Anaki+ kuderalo. Anawo anali Sesai,+ Ahimani, ndi Talimai,+ obadwa kwa Anaki.+ 15 Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a ku Debiri.+ (Zimenezi zisanachitike, Debiri ankatchedwa Kiriyati-seferi.)+ 16 Kenako Kalebe anati: “Aliyense amene agonjetse mzinda wa Kiriyati-seferi n’kuulanda, ndithu ndim’patsa mwana wanga Akisa,+ kuti akhale mkazi wake.” 17 Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ m’bale wake wa Kalebe, analanda mzindawo. Chotero Kalebe anam’patsa Akisa,+ mwana wake, kuti akhale mkazi wake. 18 Akisa ali pabulu pa ulendo wopita kunyumba, anakakamiza Otiniyeli kuti apemphe malo kwa Kalebe bambo ake. Ndiyeno Akisa anawomba m’manja kuitana bambo ake, ndipo Kalebe atamva, anam’funsa kuti: “Ukufuna chiyani?”+ 19 Iye anayankha kuti: “Ndidalitseni, poti mwandipatsa malo a kum’mwera, tsopano mundipatsenso Guloti-maimu.”* Pamenepo Kalebe anam’patsa Guloti Wakumtunda ndi Guloti Wakumunsi.+
20 Ichi chinali cholowa+ cha fuko la ana a Yuda,+ potsata mabanja awo.
21 Mizinda ya kumapeto kwa gawo la fuko la ana a Yuda, chakumalire ndi Edomu+ kum’mwera, inali Kabizeeli,+ Ederi, Yaguri, 22 Kina, Dimona, Adada, 23 Kedesi, Hazori, Itinani, 24 Zifi, Telemu,+ Bealoti, 25 Hazori-hadata, Kerioti-hezironi, kutanthauza Hazori, 26 Amamu, Sema, Molada,+ 27 Hazara-gada, Hesimoni, Beti-peleti,+ 28 Hazara-suali,+ Beere-seba,+ Bizioti, 29 Baala,+ Iimu, Ezemu,+ 30 Elitoladi, Kesili, Horima,+ 31 Zikilaga,+ Madimana, Sanasana, 32 Lebaoti, Silihimu, Aini,+ ndi Rimoni.+ Mizinda yonse inalipo 29, pamodzi ndi midzi yake.
33 Ku Sefela+ kunali Esitaoli,+ Zora,+ Asina, 34 Zanowa,+ Eni-ganimu, Tapuwa, Enamu, 35 Yarimuti,+ Adulamu,+ Soko,+ Azeka,+ 36 Saaraimu,+ Aditaimu, Gedera, ndi Gederotaimu. Mizinda 14 ndi midzi yake.
37 Zenani, Hadasha, Migidala-gadi, 38 Dilani, Mizipe, Yokiteeli, 39 Lakisi,+ Bozikati,+ Egiloni,+ 40 Kaboni, Lamamu, Kitilisi, 41 Gederoti, Beti-dagoni, Naama, ndi Makeda.+ Mizinda 16 ndi midzi yake.
42 Libina,+ Eteri,+ Asani, 43 Ifita, Asina, Nezibi, 44 Keila,+ Akizibu,+ ndi Maresha.+ Mizinda 9 ndi midzi yake.
45 Ekironi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe. 46 Kuchokera ku Ekironi kulowera chakumadzulo, malo onse amene ali m’mphepete mwa Asidodi ndi midzi yake.
47 Asidodi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe, Gaza+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe, mpaka kukafika kuchigwa cha Iguputo, ndi ku Nyanja Yaikulu pamodzi ndi dera la m’mphepete mwa nyanjayi.+
48 Kudera lamapiri kunali Samiri, Yatiri,+ Soko, 49 Dana, Kiriyati-sana, kutanthauza Debiri, 50 Anabi, Esitemo,+ Animu, 51 Goseni,+ Holoni, ndi Gilo.+ Mizinda 11 ndi midzi yake.
52 Arabu, Duma, Esana, 53 Yanimu, Beti-tapuwa, Apeka, 54 Humita, Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni,+ ndi Ziori. Mizinda 9 ndi midzi yake.
55 Maoni,+ Karimeli, Zifi,+ Yuta, 56 Yezereeli, Yokideamu, Zanowa, 57 Kayini, Gibea, ndi Timuna.+ Mizinda 10 ndi midzi yake.
58 Haluli, Beti-zuri, Gedori, 59 Maaratu, Beti-anotu, ndi Elitekoni. Mizinda 6 ndi midzi yake.
60 Kiriyati-baala,+ kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ ndi Raba. Mizinda iwiri ndi midzi yake.
61 Kuchipululu kunali Beti-araba,+ Midini, Sekaka, 62 Nibisani, Mzinda wa Mchere, ndi Eni-gedi.+ Mizinda 6 ndi midzi yake.
63 Ana a Yuda analephera kupitikitsa+ Ayebusi+ omwe anali kukhala ku Yerusalemu,+ moti Ayebusi akukhalabe limodzi ndi ana a Yuda ku Yerusalemu mpaka lero.
16 Malire a gawo+ la ana a Yosefe+ anayambira kumtsinje wa Yorodano+ kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi a Yeriko chakum’mawa, mpaka kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+ 2 Atachoka ku Beteli wa ku Luzi,+ malirewo anakadutsa kumalire a Aareki+ ku Ataroti. 3 Kenako anatsetserekera kumadzulo kumalire a Ayafeleti, mpaka kukafika kumalire a Beti-horoni Wakumunsi+ ndi Gezeri,+ n’kukathera kunyanja.+
4 Ana a Yosefe,+ omwe ndi Manase ndi Efuraimu,+ analandira gawo lawo.+ 5 Malire a kum’mawa a cholowa cha ana a Efuraimu potsata mabanja awo, anali Ataroti-adara+ mpaka kukafika ku Beti-horoni Wakumtunda,+ 6 n’kukathera kunyanja. Kumpoto kwake kunali Mikametatu,+ ndipo malirewo anazungulira chakum’mawa kukafika ku Taanatu-silo, n’kupitirirabe chakum’mawa mpaka ku Yanoa. 7 Ndiyeno anatsetsereka kuchoka ku Yanoa kukafika ku Ataroti ndi ku Naara mpaka ku Yeriko,+ n’kupitirirabe mpaka ku Yorodano. 8 Kuchoka ku Tapuwa,+ malirewo analowera chakumadzulo kuchigwa cha Kana+ n’kukathera kunyanja.+ Chimenechi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuraimu potsata mabanja awo. 9 Cholowacho chinaphatikizapo mizinda yonse ndi midzi ya ana a Efuraimu+ imene inali mkati mwa cholowa cha ana a Manase.
10 Aefuraimu analephera kupitikitsa Akanani+ amene anali kukhala ku Gezeri.+ Choncho Akananiwo akukhalabe pakati pa Aefuraimu mpaka lero,+ ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo.+
17 Fuko la Manase, mwana woyamba wa Yosefe,+ linapatsidwa gawo lake.+ Makiri+ mwana woyamba wa Manase,+ bambo wake wa Giliyadi,+ anali mwamuna wamphamvu pankhondo,+ ndipo gawo lake linali Giliyadi+ ndi Basana. 2 Ana a Manase otsalawo anapatsidwa gawo lawo potsata mabanja awo. Gawolo linapatsidwa kwa ana a Abi-ezeri,+ ana a Heleki,+ ana a Asiriyeli, ana a Sekemu,+ ana a Heferi, ndi ana a Semida.+ Amenewa anali ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, potsata mabanja awo. 3 Tselofekadi+ mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna, koma anali ndi ana aakazi. Mayina a anawo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika, ndi Tiriza.+ 4 Iwo anakaonekera pamaso pa wansembe Eleazara,+ Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri, ndi kuwauza kuti: “Yehova ndiye analamula Mose kuti atipatse cholowa pakati pa abale athu.”+ Choncho anawapatsa cholowa pakati pa abale a bambo awo, pomvera lamulo la Yehova.+
5 Fuko la Manase linapatsidwa magawo 10, kuwonjezera pa dera la Giliyadi ndi Basana lomwe linali kutsidya lina la Yorodano.+ 6 Ana aakazi a fuko la Manase anapatsidwa cholowa pakati pa ana aamuna a fukolo, ndipo dera la Giliyadi linakhala cholowa cha ana aamuna otsala a fukolo.
7 Malire a gawo la fuko la Manase anayambira ku Aseri kukafika ku Mikametatu,+ patsogolo pa Sekemu.+ Malirewo analowera kumanja kukafika kwa anthu okhala ku Eni-Tapuwa. 8 Dera la Tapuwa+ linakhala la Manase, koma mzinda wa Tapuwa umene unali m’malire a Manase, unali wa ana a Efuraimu. 9 Malire a gawolo anatsetserekera kuchigwa cha Kana. Kenaka analowera kum’mwera kwa chigwachi kumene kuli mizinda ya Efuraimu,+ yomwe ili pakati pa mizinda ya Manase. Malire a fuko la Manasewo anali kumpoto kwa chigwachi, ndipo anakathera kunyanja.+ 10 Kum’mwera kwa malirewo linali gawo la Efuraimu, ndipo kumpoto linali gawo la Manase lomwe linakathera kunyanja.+ Kumpoto, derali linakakumana ndi gawo la Aseri, ndipo kum’mawa linakakumana ndi gawo la Isakara.
11 Mizinda yotsatirayi ya m’gawo la Isakara ndi Aseri, pamodzi ndi anthu ake ndi midzi yake yozungulira, inali ya Manase:+ Beti-seani,+ Ibuleamu,+ Dori,+ Eni-dori,+ Taanaki,+ ndi Megido.+ Madera atatu amapiri analinso ake.
12 Ana a Manase analephera kulanda mizindayi,+ moti Akanani anakakamira kukhalabe m’derali.+ 13 Ana a Isiraeli atakula mphamvu,+ anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ ndipo sanathe kuwapitikitsiratu.+
14 Ana a Yosefe analankhula ndi Yoswa kuti: “N’chifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha+ kuti likhale cholowa chathu, chikhalirecho tilipo anthu ochuluka popeza Yehova watidalitsa mpaka pano?”+ 15 Yoswa atamva, anawayankha kuti: “Ngati muli ochuluka, kwerani mtunda mupite kunkhalango ya Aperezi+ ndi ya Arefai,+ mukaduleko mitengo n’kutenga deralo, chifukwa dera lamapiri+ la Efuraimu lakucheperani.” 16 Kenako ana a Yosefe anati: “Dera lamapiri silitikwanira, ndiponso Akanani a kuchigwa, a ku Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, ndiponso a kuchigwa cha Yezereeli,+ ali ndi magaleta ankhondo+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.” 17 Poyankha, Yoswa anauza anthu a fuko la Yosefe, omwe ndi Efuraimu ndi Manase, kuti: “Ndinu anthu ochuluka, ndipo ndinu amphamvu kwambiri.+ Simuyenera kukhala ndi gawo limodzi lokha,+ 18 koma mutengenso dera lamapiri.+ Poti ndi lankhalango, mudulemo mitengo ndipo gawo lanu likathere kumeneko. Mupitikitse Akanani, ngakhale kuti ndi amphamvu ndipo ali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.”+
18 Kenako khamu lonse la ana a Isiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamangako chihema chokumanako,+ popeza anali atagonjetsa dziko lomwe linali pamaso pawo.+ 2 Koma mafuko 7 a ana a Isiraeli anali asanagawiridwe cholowa. 3 Choncho Yoswa anafunsa ana a Isiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko+ limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+ 4 Sankhani amuna atatu pafuko lililonse oti ndiwatume apite akayendere dzikolo. Akalembe mmene dzikolo lilili kuti lidzagawidwe monga cholowa cha mafuko awo, akakatero adzabwerere kwa ine.+ 5 Ndiyeno adzagawane dzikolo poligawa m’zigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kum’mwera,+ ndipo a nyumba ya Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+ 6 Koma anthu inu, mukagawe dzikolo m’zigawo 7 ndipo mukazilembe. Mukakatero, mukabwere nazo kuno kwa ine kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu. 7 Alevi alibe gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni,+ ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya la kum’mawa la Yorodano.”+
8 Choncho amuna opita kukalemba dzikowo ananyamuka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula+ kuti: “Pitani mukayendere dzikolo n’kulemba mmene lilili. Mukatero mubwerere kwa ine, ndipo ineyo ndidzakuchitirani maere+ pamaso pa Yehova kuno ku Silo.”+ 9 Pamenepo amunawo anapitadi kukayendera dzikolo. Anakaligawa+ m’zigawo 7 potsatira mizinda yake, n’kulemba m’buku. Atamaliza, anapita kwa Yoswa kumsasa ku Silo, 10 ndipo Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova+ ku Silo. Kumeneko Yoswa anagawa dzikolo n’kupereka gawo limodzilimodzi ku mafuko a ana a Isiraeli.+
11 Maere+ oyamba anagwera fuko la ana a Benjamini+ potsata mabanja awo, ndipo gawo limene anapatsidwa linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+ 12 Malire a gawo lawo kumpoto anayambira ku Yorodano, n’kupitirira kukafika kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Yeriko,+ n’kukwera phiri chakumadzulo, n’kukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+ 13 Malirewo anapitirira kukafika ku Luzi,+ kutanthauza Beteli.+ Anakafika kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, n’kutsetserekera ku Ataroti-adara,+ n’kukadutsa paphiri la kum’mwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+ 14 Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kum’mwera, paphiri loyang’anizana ndi kum’mwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa ana a Yuda. Awa ndiwo malire a kumadzulo a gawo la Benjamini.
15 Malire a kum’mwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, n’kulowera chakumadzulo, n’kupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+ 16 Malirewo anatsetserekera kuphiri loyang’anizana ndi chigwa cha mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi,+ n’kutsetserekabe mpaka ku Eni-rogeli.+ 17 Analowera chakumpoto n’kukafika ku Eni-semesi mpaka ku Gelilotu, yemwe ali kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 18 Ndiyeno anakafika kumalo otsetsereka a kumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, n’kutsetserekera ku Araba. 19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Beti-hogila,+ n’kukathera kugombe la kumpoto kwa Nyanja Yamchere,+ kumapeto a kum’mwera a mtsinje wa Yorodano. Awa anali malire a kum’mwera a gawo la Benjamini. 20 Kum’mawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.
21 Mizinda ya fuko la ana a Benjamini potsata mabanja awo inali Yeriko,+ Beti-hogila, Emeki-kezizi, 22 Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+ 23 Aavi, Para, Ofira,+ 24 Kefara-amoni, Ofini, ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake.
25 Kunalinso Gibeoni,+ Rama, Beeroti, 26 Mizipe,+ Kefira,+ Moza, 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea,+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake.
Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo.+
19 Maere+ achiwiri anagwera Simiyoni, kapena kuti fuko la ana a Simiyoni,+ potsata mabanja awo. Cholowa chawo chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.+ 2 M’gawo la cholowa chawo munali Beere-seba+ kuphatikizapo Sheba, Molada,+ 3 Hazara-suali,+ Bala, Ezemu,+ 4 Elitoladi,+ Betuli, Horima, 5 Zikilaga,+ Beti-marikaboti, Hazara-susa,+ 6 Beti-lebaoti,+ ndi Saruheni. Mizinda 13 ndi midzi yake. 7 Munalinso Aini,+ Rimoni,+ Eteri, ndi Asani.+ Mizinda inayi ndi midzi yake, 8 ndiponso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka kukafika ku Baalati-beere,+ komwe ndi ku Rama+ wa kum’mwera. Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Simiyoni potsata mabanja awo. 9 Cholowa cha ana a Simiyoni chinali m’gawo la ana a Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linawakulira.+ Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+
10 Maere achitatu+ anagwera ana a Zebuloni+ potsata mabanja awo. Malire a cholowa chawo anayambira ku Saridi 11 n’kulowera chakumadzulo, kukafika ku Marala. Anapitirira kukafika ku Dabeseti mpaka kuchigwa chimene chili kutsogolo kwa Yokineamu.+ 12 Kenako malirewo anakhota n’kubwerera kulowera kum’mawa kwa Saridi mpaka kumalire a Kisilotu-tabori. Ndiyeno anapitirira kukafika ku Daberati+ mpaka ku Yafiya. 13 Kuchokera kumeneko, malirewo analowera chakum’mawa n’kukafika ku Gati-heferi,+ ku Eti-kazini, ndi ku Rimoni, mpaka ku Nea. 14 Malirewo anazungulira kumpoto kwa Nea kukafika ku Hanatoni, n’kukathera kuchigwa cha Ifita-eli, 15 komanso ku Katati, Nahalala, Simironi,+ Idala, ndi ku Betelehemu.+ Mizindayi inalipo 12 ndi midzi yake. 16 Ichi chinali cholowa+ cha ana a Zebuloni potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
17 Maere achinayi anagwera Isakara,+ kapena kuti ana a Isakara potsata mabanja awo. 18 Malire a gawo lawo anakafika ku Yezereeli,+ Kesulotu, Sunemu,+ 19 Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20 Rabiti, Kisioni, Ebezi, 21 Remeti, Eni-ganimu,+ Eni-hada, ndi Beti-pazezi. 22 Malirewo anakafika ku Tabori,+ ku Sahazuma, ndi ku Beti-semesi n’kukathera ku Yorodano. Mizinda 16 ndi midzi yake. 23 Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Isakara potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
24 Maere achisanu+ anagwera fuko la ana a Aseri,+ potsata mabanja awo. 25 Malire a gawo lawo anadutsa ku Helikati,+ Hali, Beteni, Akasafu,+ 26 Alameleki, Amadi, ndi Misali.+ Analowera chakumadzulo ku Karimeli+ ndi ku Sihori-libanati. 27 Kenako anakhota n’kubwerera kulowera kotulukira dzuwa ku Beti-dagoni, n’kukafika ku Zebuloni+ ndi kumpoto kwa chigwa cha Ifita-eli. Anakafikanso ku Beti-emeki ndi ku Nehieli n’kupitirira mpaka ku Kabulu chakumanzere. 28 Anapitirira mpaka ku Eburoni, Rehobu, Hamoni, Kana, mpaka kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni.+ 29 Malirewo anakhota n’kubwerera ku Rama, mpaka kukafika kumzinda wa Turo+ wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako anakhotanso n’kubwerera ku Hosa n’kukathera kunyanja, m’chigawo cha Akizibu.+ 30 Anakafikanso ku Uma, Afeki,+ ndi Rehobu.+ Mizindayi inalipo 22 ndi midzi yake. 31 Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Aseri potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
32 Maere a 6+ anagwera ana a Nafitali+ potsata mabanja awo. 33 Malire a gawo lawo anayambira ku Helefi, ndi kumtengo waukulu wa ku Zaananimu,+ mpaka ku Adami-nekebi, ndi ku Yabineeli, n’kukafika ku Lakumu n’kukathera ku Yorodano. 34 Malirewo anakhotera kumadzulo n’kubwerera ku Azinotu-tabori, n’kupitirira mpaka kukafika ku Hukoku ndi ku Zebuloni+ kum’mwera. Anakafikanso ku Aseri+ kumadzulo, ndi kotulukira dzuwa ku Yuda,+ kumtsinje wa Yorodano. 35 Mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri inali Zidimu, Zere, Hamati,+ Rakati, Kinereti,+ 36 Adama, Rama, Hazori,+ 37 Kedesi,+ Edirei, Eni-hazori, 38 Yironi, Migidala-eli, Horemu, Beti-anati, ndi Beti-semesi.+ Mizinda 19 ndi midzi yake. 39 Ichi chinali cholowa+ cha fuko la ana a Nafitali potsata mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
40 Maere a 7+ anagwera fuko la ana a Dani+ potsata mabanja awo. 41 Malire a gawo la cholowa chawo anadutsa ku Zora,+ Esitaoli, Iri-semesi, 42 Saalabini,+ Aijaloni,+ Itila, 43 Eloni, Timuna,+ Ekironi,+ 44 Eliteke, Gebetoni,+ Baalati,+ 45 Yehuda, Bene-beraki, Gati-rimoni,+ 46 Me-jarikoni, Rakoni, n’kukafika kumalire amene ali kutsogolo kwa Yopa.+ 47 Gawo la ana a Dani linawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo n’kupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga n’kuyamba kukhalamo ndipo anautcha Lesemu Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ 48 Ichi chinali cholowa cha fuko la ana a Dani potsata mabanja awo, ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.
49 Apa m’pamene anamalizira kugawa dzikolo m’zigawozigawo kuti akhalemo. Kenako ana a Isiraeli anam’patsa cholowa Yoswa mwana wa Nuni pakati pawo. 50 Molamulidwa ndi Yehova, anam’patsa mzinda umene anapempha+ wa Timinati-sera,+ m’dera lamapiri la Efuraimu ndipo iye anayamba kumanga mzindawo n’kumakhalamo.
51 Zimenezi ndiye zigawo za cholowa chimene wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli, anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako,+ ndipo anamaliza kuligawa dzikolo.
20 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ mogwirizana ndi zimene ndinakuuzani kudzera mwa Mose. 3 Mizindayo ntchito yake ikhale yoti wopha munthu+ mwangozi azithawirako pothawa wobwezera magazi.+ 4 Azithawira+ kumzinda umodzi mwa mizindayi n’kukaima pachipata+ cholowera mumzindawo. Akatero azifotokoza nkhani yake kwa akulu+ a mzindawo. Akuluwo amulandire n’kumupatsa malo mumzindamo kuti azikhala nawo limodzi. 5 Ngati wobwezera magazi atam’thamangitsa, akuluwo asapereke wopha munthuyo m’manja mwa wobwezera magaziyo,+ chifukwa iye sanaphe munthu mnzakeyo mwadala, ndiponso sankadana naye.+ 6 Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,+ komanso mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Izi zikachitika, wopha munthuyo akhoza kubwerera kwawo,+ n’kukalowa m’nyumba mwake, mumzinda momwe anathawamo muja.’”
7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda. 8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.
9 Imeneyi inali mizinda imene inasankhidwa kuti ana a Isiraeli onse ndi alendo okhala pakati pawo, azithawirako akapha munthu mwangozi,+ kuti asaphedwe ndi wobwezera magazi mpaka akaonekere pamaso pa oweruza.+
21 Tsopano atsogoleri a mabanja a Alevi, anapita kwa wansembe Eleazara,+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli. 2 Analankhula nawo ku Silo+ m’dziko la Kanani, kuti: “Kudzera mwa Mose, Yehova analamula kuti tipatsidwe mizinda yoti tizikhalamo, pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayo, oti tizidyetserako ziweto zathu.”+ 3 Choncho ana a Isiraeli pomvera lamulo la Yehova, anapatsa Alevi+ mizindayo ndi malo ake odyetserako ziweto, kuchokera pa cholowa chawo.+
4 Atachita maere, maerewo anagwera mabanja a Akohati.+ Choncho mizinda 13 inakhala ya ana a wansembe Aroni, omwe anali Alevi. Mizinda yake inachokera m’mafuko a Yuda,+ Simiyoni,+ ndi Benjamini.+
5 Anachita maere ena, ndipo ana a Kohati+ amene anatsala anawapatsa mizinda 10 yochokera m’mabanja a fuko la Efuraimu,+ Dani,+ ndi hafu ya fuko la Manase.+
6 Anachitanso maere, ndipo ana a Gerisoni+ anapatsidwa mizinda 13 yochokera m’mabanja a fuko la Isakara,+ Aseri,+ Nafitali,+ ndi hafu ya fuko la Manase ku Basana.+
7 Ana a Merari+ anapatsidwa mizinda 12 yochokera m’fuko la Rubeni,+ Gadi,+ ndi Zebuloni,+ potsata mabanja awo.
8 Chotero ana a Isiraeli anapatsa Alevi mizinda imeneyi ndi malo ake odyetserako ziweto,+ mwa kuchita maere.+ Anachita zimenezi monga mmene Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose.+
9 Ana a Isiraeli anapereka mizinda, kuchokera m’fuko la ana a Yuda ndi fuko la ana a Simiyoni. Mizindayo anachita kuitchula mayina.+ 10 Mizinda yotsatirayi inakhala ya ana a Aroni ochokera m’mabanja a Akohati, omwe anali ana a Levi, chifukwa maere oyamba anagwera iwowa.+ 11 Anawapatsa Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali tate wa Anaki.)+ Mzindawu, pamodzi ndi malo ouzungulira odyetserako ziweto, unali m’dera lamapiri la Yuda.+ 12 Malo ozungulira mzindawo ndi midzi yake, anawapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune kuti akhale ake.+
13 Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu+ amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 14 Yatiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 15 Holoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 16 Aini+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yuta+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beti-semesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda 9, kuchokera m’mafuko awiri amenewa.
17 Kuchokera m’fuko la Benjamini, anawapatsa Gibeoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Geba+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 18 Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Alimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
19 Mizinda yonse ya ansembe, ana a Aroni,+ inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto.+
20 Mabanja a ana a Kohati, kapena kuti Alevi otsala pa ana a Kohati, anapatsidwa mizinda yochokera m’fuko la Efuraimu. Iwo anapatsidwa mizindayi pambuyo pochita maere.+ 21 Motero anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 22 Kibizaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
23 Kuchokera m’fuko la Dani, anawapatsa Eliteke ndi malo ake odyetserako ziweto, Gebetoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 24 Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Gati-rimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
25 Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anawapatsa Taanaki+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.
26 Mizinda yonse pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto, imene mabanja a ana otsala a Kohati anapatsidwa, inalipo 10.
27 Ana a Gerisoni+ a m’mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase.+ Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana, ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beesitera+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.
28 Kuchokera m’fuko la Isakara,+ anawapatsa Kisioni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 29 Yarimuti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Eni-ganimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
30 Kuchokera m’fuko la Aseri,+ anawapatsa Misali+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Abidoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 31 Helikati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
32 Kuchokera m’fuko la Nafitali,+ anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Kedesi,+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu.
33 Mizinda yonse ya Agerisoni potsata mabanja awo inalipo 13, ndi malo ake odyetserako ziweto.
34 Kuchokera m’fuko la Zebuloni,+ mabanja a ana a Merari,+ amene ndi Alevi otsala, anapatsidwa Yokineamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Karita ndi malo ake odyetserako ziweto, 35 Dimena+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Nahalala+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
36 Kuchokera m’fuko la Rubeni,+ anawapatsa Bezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 37 Kademoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Mefaata+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
38 Kuchokera m’fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi,+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 39 Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi.
40 Ana a Merari,+ omwe anatsala pa mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda yokwana 12 potsata mabanja awo, mwa kuchita maere.
41 Mizinda yonse ya Alevi m’dziko limene ana a Isiraeli anapatsidwa inalipo 48,+ pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 42 Mzinda uliwonse pa mizinda imeneyi unazunguliridwa ndi malo odyetserako ziweto. Ndi mmene mizinda yonseyi inalili.+
43 Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,+ ndipo iwo analanda+ dzikolo n’kumakhalamo. 44 Kuwonjezera apo, Yehova anawapatsa mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira+ makolo awo. Panalibe ngakhale mdani mmodzi pa adani awo onse amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse m’manja mwawo.+ 45 Palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.+
22 Pa nthawi imeneyo, Yoswa anaitana Arubeni, Agadi ndi hafu ya fuko la Manase,+ 2 n’kuwauza kuti: “Inu mwasunga zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani,+ ndiponso mwamvera mawu anga m’zonse zimene ndakulamulirani.+ 3 Simunawasiye abale anu masiku onsewa+ kufikira lero, ndipo mwasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ 4 Tsopano Yehova Mulungu wanu wapatsa abale anu mpumulo monga momwe anawalonjezera.+ Chotero bwererani, mupite kumahema anu m’dziko lanu, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani kutsidya lina la Yorodano.+ 5 Koma mukaonetsetse kuti mukusunga malamulo+ ndi Chilamulo chimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani. Mukachite zimenezi mwa kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda m’njira zake zonse,+ kusunga malamulo ake,+ kum’mamatira,+ ndiponso kum’tumikira+ ndi mtima wanu wonse+ ndiponso moyo wanu wonse.”+
6 Atatero, Yoswa anawadalitsa+ n’kuwauza kuti azipita kumahema awo. 7 Mose anali atapatsa hafu ya fuko la Manase cholowa ku Basana.+ Hafu ina ya fukolo, Yoswa anaipatsa cholowa pamodzi ndi abale awo kutsidya lina la Yorodano kumadzulo.+ Ndipo Yoswa anawadalitsa pamene anawauza kuti azipita kumahema awo. 8 Anawauza kuti: “Bwererani kumahema anu ndi chuma chambiri ndiponso ziweto zambiri, ndi siliva, golide, mkuwa, zitsulo, ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munafunkha+ kwa adani anu n’kugawana ndi abale anu.”
9 Zitatero, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase, anachoka ku Silo kumene kunali ana ena a Isiraeli m’dziko la Kanani. Anapita ku Giliyadi,+ dziko lawo limene anapatsidwa ndi Mose molamulidwa ndi Yehova, ndiponso limene anakhazikikamo.+ 10 Atafika kuchigawo cha Yorodano chimene chinali m’dziko la Kanani, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase anamanga guwa lansembe m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano, ndipo guwalo+ linali lalikulu zedi. 11 Kenako ana ena a Isiraeli anauzidwa+ kuti: “Tamverani! Ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase amanga guwa lansembe m’malire a dziko la Kanani, m’chigawo cha Yorodano kumbali ya ana a Isiraeli.” 12 Ana a Isiraeli atamva zimenezi, khamu lawo lonse+ linasonkhana ku Silo+ kuti apite kukawathira nkhondo.+
13 Kenako ana a Isiraeli anatumiza+ Pinihasi+ mwana wa wansembe Eleazara, kwa ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase, ku Giliyadi. 14 Anam’tumiza pamodzi ndi atsogoleri 10. Fuko lililonse la Isiraeli linatumiza mtsogoleri mmodzi woimira nyumba ya makolo ake. Mtsogoleri aliyense anali woimira nyumba ya bambo ake pakati pa Aisiraeli masauzande.+ 15 Anthuwo anafika kwa ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi, n’kuyamba kuwauza+ kuti:
16 “Khamu lonse la Yehova+ lati, ‘N’chifukwa chiyani mwachita zosakhulupirika+ kulakwira Mulungu wa Isiraeli? N’chifukwa chiyani lero mwatembenuka n’kusiya+ kutsatira Yehova podzimangira guwa lansembe+ kuti mupandukire Yehova? 17 Kodi cholakwa chimene tinachita ku Peori+ chatichepera? Kufikira lero, sitinadziyeretsebe ku cholakwa chimene chija, ngakhale kuti mliri unagwera khamu la Yehova.+ 18 Kodi inuyo tsopano mukufuna kubwerera n’kusiya kutsatira Yehova? Mukapandukira Yehova lero, ndiye kuti mawa adzakwiyira khamu lonse la Isiraeli.+ 19 Ngati n’zoona kuti dziko lanu n’lodetsedwa,+ wolokerani kudziko la Yehova+ kumene kuli chihema chopatulika cha Yehova,+ mukakhazikike pakati pathu. Koma musapandukire Yehova, ndipo musachititse ifeyo kupanduka chifukwa cha guwa lansembe limene mwamangali, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu.+ 20 Kodi Akani+ mwana wa Zera sanachite zosakhulupirika pa chinthu choyenera kuwonongedwa? Kodi mkwiyo sunagwere khamu lonse la Isiraeli?+ Komatu iye sanafe yekha chifukwa cha cholakwa chakecho.’”+
21 Atamva zimenezi, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase anayankha+ atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, kuti:+ 22 “Wamphamvu,+ Mulungu,+ Yehova,+ Wamphamvu, Mulungu, Yehova, iye akudziwa,+ ndipo nayenso Isiraeli adziwa.+ Ngati tachita zimenezi chifukwa chopanduka+ ndiponso chifukwa cha kusakhulupirika pamaso pa Yehova,+ musatisiye amoyo lero. 23 Ngati tadzimangira guwa lansembe kuti titembenuke n’kusiya kutsatira Yehova, ndipo ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zopsereza ndi nsembe zambewu,+ ndiponso ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zachiyanjano, Yehova afufuza yekha.+ 24 Koma ife tinamanga guwa lansembeli chifukwa choda nkhawa kuti, ‘Tsiku lina m’tsogolo muno ana anu adzauza ana athu kuti: “Inu muli naye chiyani Yehova Mulungu wa Isiraeli? 25 Yehova waika malire pakati pa ife ndi inuyo ana a Rubeni ndi ana a Gadi. Malire ake ndi mtsinje wa Yorodano. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.”+ Chotero ana anu adzachititsa ana athu kusiya kuopa Yehova.’+
26 “Choncho tinati, ‘Tsopano tiyeni tichitepo kanthu kumbali yathu mwa kumanga guwa, osati loperekerapo zopereka kapena nsembe zopsereza, 27 koma kuti likhale mboni pakati pa ife+ ndi inu ndi mibadwo yobwera pambuyo pathu. Guwalo likhale mboni yakuti tidzatumikira Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, nsembe zachiyanjano ndi nsembe zina,+ kuti tsiku lina m’tsogolo ana anu asadzanene kwa ana athu kuti: “Inu mulibe gawo mwa Yehova.”’ 28 Chotero tinati, ‘Akadzanena zimenezi kwa ife ndi kwa mibadwo yathu m’tsogolo, ifenso tidzati: “Taonani chifaniziro cha guwa lansembe la Yehova chimene makolo athu anamanga, osati choperekerapo zopereka kapena nsembe zopsereza, koma monga mboni ya pakati pa ife ndi inu.”’ 29 N’zosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova+ mwadala, n’kuleka kutsatira Yehova mwa kumanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa chihema chake chopatulika!”+
30 Wansembe Pinihasi,+ atsogoleri a khamu la Aisiraeli+ kapena kuti atsogoleri a masauzande a Aisiraeli amene anali naye, atamva mawu amene ana a Rubeni, ana a Gadi ndi ana a Manase ananena, anakhutira nawo mawuwo. 31 Ndiyeno Pinihasi mwana wa wansembe Eleazara, anauza ana a Rubeni, ana a Gadi ndi ana a Manase, kuti: “Lero tadziwa kuti Yehova ali pakati pathu+ chifukwa simunapandukire Yehova. Tsopano mwalanditsa ana a Isiraeli m’dzanja la Yehova.”+
32 Pamenepo, Pinihasi mwana wa wansembe Eleazara ndi atsogoleri aja, anachoka kwa ana a Rubeni ndi ana a Gadi m’dziko la Giliyadi, n’kubwerera+ kwa ana ena a Isiraeli kudziko la Kanani. Kumeneko, iwo anawafotokozera zimene ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena.+ 33 Ana a Isiraeli atamva mawuwo, anakhutira nawo ndipo anatamanda Mulungu.+ Ndipo sananenenso zopita kukamenyana ndi ana a Rubeni ndi ana a Gadi, ndi kuwononga dziko limene iwo anali kukhalamo.
34 Ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha dzina guwalo.* Iwo anati, “Guwali ndi mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu woona.”+
23 Tsopano Yoswa anali atakalamba ndiponso anali ndi zaka zambiri.+ Apa n’kuti patapita masiku ambiri kuchokera pamene Yehova anapatsa Aisiraeli mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira. 2 Pa nthawiyo, Yoswa anaitana Aisiraeli onse+ ndi akulu awo, omwe anali atsogoleri awo, oweruza awo, ndi akapitawo awo,+ n’kuwauza kuti: “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri. 3 Inuyo mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu anachitira mitundu yonse chifukwa cha inu.+ Yehova Mulungu wanu ndiye anali kukumenyerani nkhondo.+ 4 Taonani, ndinakupatsani malo a mitundu yonse imene yatsalayi mwa kuchita maere.+ Ndinakupatsaninso malo a mitundu imene ndinaiwononga+ kuchokera kumtsinje wa Yorodano, mpaka kolowera dzuwa, ku Nyanja Yaikulu, monga cholowa cha mafuko anu.+ 5 Yehova Mulungu wanu ndiye anali kuwathamangitsa pamaso panu,+ ndipo anawapitikitsa chifukwa cha inu. Pamenepo, inu munatenga malo awo monga mmene Yehova Mulungu wanu anakulonjezerani.+
6 “Tsopano khalani olimba mtima kwambiri,+ kuti musunge ndi kuchita zonse zimene zinalembedwa m’buku+ la chilamulo cha Mose, posapatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 7 Ndiponso musayanjane ndi mitundu+ imene yatsala pakati panu. Musamatchule mayina a milungu yawo+ kapena kulumbirira pa milunguyo,+ ndipo musamaitumikire kapena kuigwadira.+ 8 Koma mamatirani+ Yehova Mulungu wanu monga mmene mwakhala mukuchitira kufikira lero. 9 Yehova adzapitikitsa mitundu ikuluikulu ndiponso yamphamvu kuichotsa pamaso panu.+ (Kufikira lero, palibe munthu ngakhale mmodzi amene wakwanitsa kulimbana nanu.)+ 10 Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo,+ monga mmene anakulonjezerani.+ 11 Muzikonda Yehova Mulungu wanu,+ ndipo potero tetezani miyoyo yanu nthawi zonse.+
12 “Koma mukatembenuka+ n’kumamatira zotsala za anthu awa a mitundu ina,+ amene atsala pakati panuwa, kumakwatirana nawo,+ n’kumakhala pakati pawo, iwonso n’kumakhala pakati panu, 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzaleka kuwapitikitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu.+ Adzakhalanso ngati zokubayani* m’mbali mwanu komanso ngati zitsotso m’maso mwanu, kufikira mutatheratu padziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+
14 “Tsopano taonani! Ine ndatsala pang’ono kufa.+ Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+ 15 Mawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu analankhula akwaniritsidwa pa inu,+ momwemonso Yehova adzakwaniritsa pa inu mawu onse oipa, kufikira atakufafanizani kukuchotsani padziko labwinoli, limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 16 Adzatero chifukwa chakuti mwaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, ndiponso chifukwa chakuti mwapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani+ ndipo mudzatha mwamsanga padziko labwino limene iye anakupatsani.”+
24 Ndiyeno Yoswa anasonkhanitsa pamodzi mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu.+ Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli,+ atsogoleri, oweruza, ndi akapitawo, ndipo iwo anaima pamaso pa Mulungu woona.+ 2 Tsopano Yoswa anauza anthu onse kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kalekale, makolo anu,+ kuphatikizapo Tera, bambo ake a Abulahamu ndi Nahori,+ ankakhala kutsidya lina la Mtsinje,*+ ndipo ankatumikira milungu ina.
3 “‘Patapita nthawi, ndinatenga Abulahamu+ tate wanu, kuchokera kutsidya lina la Mtsinje,+ ndipo ndinamuyendetsa m’dziko lonse la Kanani, ndi kuchulukitsa mbewu yake.+ Chotero ndinam’dalitsa ndipo anabereka Isaki,+ 4 Isaki anabereka Yakobo ndi Esau.+ Pambuyo pake Esau ndinam’patsa phiri la Seiri kuti likhale lake.+ Kenako, Yakobo ndi ana ake anapita ku Iguputo.+ 5 Patapita nthawi, ndinatumiza Mose ndi Aroni,+ ndipo ndinagwetsera Iguputo miliri.+ Nditatero ndinakutulutsani+ ku Iguputoko. 6 Pamene ndinali kutulutsa makolo anu ku Iguputo,+ atatsala pang’ono kufika kunyanja, Aiguputo anawathamangira+ ndi magaleta ankhondo ndiponso amuna okwera pamahatchi, mpaka ku Nyanja Yofiira. 7 Pamenepo, iwo anayamba kufuulira Yehova.+ Choncho ine ndinaika mdima pakati pa iwo ndi Aiguputuwo,+ ndipo ine ndinawamiza ndi madzi a m’nyanja.+ Munaona ndi maso anu zimene ndinachita ku Iguputo.+ Kenako, inu munakhala m’chipululu masiku ambiri.+
8 “‘Pamapeto pake, ndinakufikitsani kudziko la Aamori amene anali kukhala kutsidya lina la Yorodano. Iwo anayamba kumenyana nanu,+ koma ine ndinawapereka m’manja mwanu kuti mutenge dziko lawo kukhala lanu. Chotero ndinawafafaniza kuwachotsa pamaso panu.+ 9 Kenako Balaki mwana wa Zipori,+ mfumu ya Mowabu, ananyamuka kukamenyana ndi Isiraeli.+ Iye anaitanitsa Balamu, mwana wa Beori, ndi kumuuza kuti akutemberereni.+ 10 Ine sindinafune kumvera Balamu.+ Chotero, iye anakudalitsani mobwerezabwereza,+ ndipo ine ndinakulanditsani m’manja mwake.+
11 “‘Kenako munawoloka Yorodano+ n’kufika ku Yeriko.+ Nzika za ku Yeriko, Aamori, Aperezi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi anayamba kumenyana nanu, koma ine ndinawapereka m’manja mwanu.+ 12 Ndinawachititsa mantha inu musanafike, choncho anakuthawani+ monga anachitira mafumu awiri a Aamori. Iwo sanathawe chifukwa cha lupanga lanu kapena chifukwa cha uta wanu.+ 13 Chotero ndinakupatsani dziko limene simunakhetsere thukuta ndi mizinda imene simunamange,+ ndipo inu munayamba kukhalamo. Ndiponso mukudya zipatso za mitengo ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunabzale.’+
14 “Tsopano opani Yehova+ ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo,+ ndipo tumikirani Yehova. 15 Ngati kutumikira Yehova kukukuipirani, sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira,+ kaya milungu imene makolo anu amene anali kutsidya lina la Mtsinje anatumikira,+ kapena milungu ya Aamori amene mukukhala m’dziko lawo.+ Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”+
16 Pamenepo, anthuwo anayankha kuti: “Sitingayerekeze kusiya Yehova, kuti tizitumikira milungu ina. 17 Pakuti ndi Yehova Mulungu wathu amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo+ pamodzi ndi makolo athu, kutichotsa m’nyumba yaukapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza m’njira yonse imene tinayenda, ndiponso kwa mitundu yonse ya anthu amene tinadutsa pakati pawo.+ 18 Yehova anathamangitsa mitundu yonse ya anthu+ pamaso pathu, ngakhale Aamori amene anali kukhala m’dzikoli. Choncho, nafenso tizitumikira Yehova chifukwa iye ndi Mulungu wathu.”+
19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+ 20 Mukasiya Yehova+ n’kuyamba kutumikira milungu yachilendo,+ iyenso adzakutembenukirani ndithu, n’kukuchitirani zoipa ndi kukufafanizani, pambuyo pokuchitirani zabwino.”+
21 Poyankha, anthuwo anauza Yoswa kuti: “Ayi! Ife tizitumikira Yehova.”+ 22 Pamenepo Yoswa anauza anthuwo kuti: “Inu ndinu mboni mwa kufuna kwanu,+ zotsimikizira kuti mwasankha nokha kutumikira Yehova.”+ Ndiyeno anthuwo anati: “Inde! Ndife mboni.”
23 “Tsopano chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu,+ ndipo tembenuzirani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.” 24 Ndiyeno anthuwo anamuyankha Yoswa kuti: “Tizitumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mawu ake!”+
25 Pa tsikulo, Yoswa anachita pangano ndi anthuwo ndi kuwaikira lamulo ndi chigamulo+ ku Sekemu. 26 Ndiyeno Yoswa analemba mawu amenewa m’buku la chilamulo cha Mulungu.+ Atatero, anatenga mwala waukulu+ ndi kuuika pansi pa mtengo waukulu kwambiri+ umene uli pafupi ndi malo opatulika a Yehova.
27 Kenako Yoswa anauza anthu onsewo kuti: “Taonani! Mwala uwu ukhala mboni yotsutsana nafe,+ chifukwa mwalawu wamva mawu onse amene Yehova walankhula kwa ife, ndipo ukhala mboni kwa inu kuti musadzakane Mulungu wanu.” 28 Atatero, Yoswa anauza anthuwo kuti azipita, aliyense kucholowa chake.+
29 Patapita nthawi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 30 Choncho anamuika m’manda m’gawo la cholowa chake ku Timinati-sera,+ kudera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 31 Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira,+ omwe ankadziwa ntchito zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.+
32 Mafupa a Yosefe,+ amene ana a Isiraeli anabweretsa kuchokera ku Iguputo anawaika m’manda ku Sekemu, pamalo amene Yakobo anagula kwa ana a Hamori,+ tate wa Sekemu. Malowo anawagula ndi ndalama zasiliva zokwana 100,+ ndipo anakhala a ana a Yosefe monga cholowa chawo.+
33 Nayenso Eleazara mwana wa Aroni anamwalira.+ Choncho anamuika m’manda m’phiri la Pinihasi mwana wake,+ limene anapatsidwa m’dera lamapiri la Efuraimu.
Kapena kuti “patsindwi.”
Fulakesi ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “kwa ife.”
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Dzina lakuti “Akori” limatanthauza “Kunyanyalidwa” kapena “Mavuto.”
Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.
Mawu ake enieni, “mpweya uliwonse.”
M’Baibulo, “nyanja ya Kinereti” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Genesarete,” “nyanja ya Galileya” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Anali ‘kuwapundula’ mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wakumbuyo.
Onani mawu a m’munsi a pa Ge 26:17.
Mawu akuti “Guloti-maimu” amatanthauza “Zigwa za Madzi.”
Guwalo ayenera kuti analitcha dzina lakuti, “Mboni.”
Ena amati “kulasa.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mawu ake enieni, “m’choonadi.”