Chivumbulutso kwa Yohane
1 Chivumbulutso+ choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa,+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.+ Yesuyo anatumiza mngelo wake+ kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro+ kwa kapolo wake Yohane.+ 2 Yohaneyo anachitira umboni mawu a Mulungu,+ ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka,+ kutanthauza zonse zimene anaona. 3 Wodala+ ndi munthu amene amawerenga mokweza,+ ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu,+ komanso amene akusunga zolembedwamo,+ pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.+
4 Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7+ ya m’chigawo cha Asia.
Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,”+ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7+ yokhala pamaso pa mpando wake wachifumu. 5 Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,”+ ndiponso “Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.”+
Kwa iye amene amatikonda,+ amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo,+ 6 n’kutipanga kukhala mafumu+ ndi ansembe+ kwa Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya.+ Ame.
7 Taonani! Akubwera ndi mitambo,+ ndipo diso lililonse lidzamuona,+ ngakhalenso anthu amene anamulasa.+ Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye.+ Ame.
8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,”*+ akutero Yehova Mulungu, “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,+ Wamphamvuyonse.”+
9 Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso+ a Yesu,+ mu ufumu+ ndi m’kupirira,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.+ 10 Mwa mzimu,+ ndinapezeka kuti ndili+ m’tsiku la Ambuye,+ ndipo kumbuyo kwanga ndinamva mawu amphamvu+ ngati kulira kwa lipenga. 11 Mawuwo anali akuti: “Zimene uone, lemba+ mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7+ yotsatirayi: wa ku Efeso,+ wa ku Simuna,+ wa ku Pegamo,+ wa ku Tiyatira,+ wa ku Sade,+ wa ku Filadefiya,+ ndi wa ku Laodikaya.”+
12 Ndinacheuka kuti ndione, kuti ndani amene anali kundilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.+ 13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi, atamanga lamba wagolide pachifuwa. 14 Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera+ ngati ubweya wa nkhosa woyera, zoyera kwambiri kuti mbee! Ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.+ 15 Mapazi ake anali ngati mkuwa woyengedwa+ bwino ukamanyezimira m’ng’anjo, ndipo mawu+ ake anali ngati mkokomo wa madzi ambiri. 16 M’dzanja lake lamanja anali ndi nyenyezi 7.+ M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ Nkhope yake inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.+ 17 Nditamuona, ndinagwa pamapazi ake ngati kuti ndafa.
Ndipo anandigwira ndi dzanja lake lamanja ndi kundiuza kuti: “Usachite mantha.+ Ine ndine Woyamba+ ndi Wotsiriza,+ 18 ndiponso wamoyo.+ Ndinali wakufa,+ koma taona, ndili ndi moyo kwamuyaya,+ ndipo ndili ndi makiyi a imfa+ ndi a Manda.*+ 19 Choncho lemba zimene waona, zimene zikuchitika panopa, ndi zimene zidzachitike pambuyo pa zimenezi.+ 20 Koma za chinsinsi chopatulika cha nyenyezi 7,+ zimene waona m’dzanja langa lamanja, ndi za chinsinsi cha zoikapo nyale 7 zagolide,+ tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi 7, zikuimira angelo* a mipingo 7, ndipo zoikapo nyale 7, zikuimira mipingo 7.+
2 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Efeso,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena wonyamula nyenyezi 7+ m’dzanja lake lamanja, woyenda pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide.+ 2 ‘Ndikudziwa ntchito zako,+ khama lako, ndi kupirira kwako, ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Iwe unayesanso+ anthu amene amadzitcha atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama. 3 Umaonetsanso kupirira,+ ndipo walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa,+ koma sunafooke.+ 4 Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.+
5 “‘Choncho, kumbukira malo amene unali usanagwe, lapa+ ndi kuchita ntchito za poyamba. Ngati sutero, ndikubwera kwa iwe,+ ndipo ndidzachotsa choikapo nyale chako+ pamalo ake ngati sulapa. 6 Komabe, pali chinthu chimodzi chimene ukuchita bwino: Umadana+ ndi ntchito za mpatuko wa Nikolao,+ zimenenso ine ndimadana nazo. 7 Ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo,+ ndidzamulola kudya za mumtengo wa moyo,+ umene uli m’paradaiso wa Mulungu.’
8 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Simuna lemba kuti: Izi ndi zimene akunena ‘Woyamba ndi Wotsiriza,’+ amene anafa n’kukhalanso ndi moyo.+ 9 ‘Ndikudziwa masautso ako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.+ Ndikudziwanso za kutonza kwa odzitcha Ayudawo,+ pamene si Ayuda, koma ndiwo sunagoge wa Satana.+ 10 Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.+ Taona! Mdyerekezi+ adzapitiriza kuponya m’ndende ena a inu, kuti muyesedwe mpaka pamapeto,+ ndipo mudzakhala m’masautso+ masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa,+ ndipo ndidzakupatsa mphoto* ya moyo.+ 11 Ali ndi makutu amve+ zimene mzimu+ ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo,+ sadzakhudzidwa ndi imfa yachiwiri.’+
12 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Pegamo lemba kuti: Izi ndi zimene akunena amene ali ndi lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ 13 ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa,+ ndipo sunakane kuti umakhulupirira ine.+ Sunakane ngakhale m’masiku a Antipa mboni yanga,+ wokhulupirika wanga uja, amene anaphedwa+ pambali panu, kumene Satana akukhala.
14 “‘Koma ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.+ 15 Ndiponso uli ndi olimbikira chiphunzitso cha mpatuko wa Nikolao.+ 16 Choncho ulape.+ Ngati sulapa, ndikubwera kwa iwe msanga, ndipo ndidzamenyana+ nawo ndi lupanga lalitali la m’kamwa mwanga.+
17 “‘Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Wopambana pa nkhondo+ ndidzamupatsa ena mwa mana+ obisika. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwa dzina latsopano+ limene wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.’+
18 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Tiyatira+ lemba kuti: Izi ndi zimene Mwana+ wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi la moto,+ ndipo mapazi ake ali ngati mkuwa woyengedwa bwino.+ 19 ‘Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako,+ chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako+ zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.+
20 “‘Komabe, ndakupeza ndi mlandu uwu. Walekerera mayi uja Yezebeli,+ amene amadzitcha mneneri. Iye amaphunzitsa+ ndi kusocheretsa akapolo anga+ kuti azichita dama+ ndi kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano.+ 21 Ndamupatsa nthawi kuti alape,+ koma sakufuna kulapa dama* lake.+ 22 Taona! Ndatsala pang’ono kumudwalitsa kwambiri, ndipo ochita naye chigololo ndiwaponya m’masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo. 23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+
24 “‘Komabe, kwa ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene mulibe chiphunzitso chimenechi, amene simudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amazitcha “zinthu zozama za Satana,”+ ndikuti: Sindikusenzetsani katundu wina wolemera.+ 25 Gwirani mwamphamvu zomwe zija, zimene muli nazo,+ mpaka nditabwera. 26 Ndipo amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto,+ ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu.+ 27 Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo,+ ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.+ 28 Ndidzamupatsanso nthanda.*+ 29 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’+
3 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Sade, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena iye amene ali ndi mizimu 7+ ya Mulungu, ndi nyenyezi 7.+ ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti uli ndi dzina lakuti uli moyo, pamene ndiwe wakufa.+ 2 Khala maso,+ ndipo limbikitsa+ otsala amene atsala pang’ono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga.+ 3 Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira+ ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira,+ ndipo ulape.+ Ndithudi, ukapanda kudzuka,+ ndidzabwera ngati mbala,+ ndipo sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.+
4 “‘Ngakhale zili choncho, uli ndi mayina+ angapo mu Sade a anthu amene sanaipitse+ malaya awo akunja. Amenewa adzayenda ndi ine atavala malaya oyera,+ chifukwa ndi oyenerera.+ 5 Choncho amene wapambana pa nkhondo+ adzavekedwa malaya akunja oyera.+ Ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo,+ koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga,+ ndi pamaso pa angelo ake.+ 6 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena+ ku mipingo.’
7 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Filadefiya, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena woyerayo,+ amene ali woona,+ yemwe ali ndi kiyi wa Davide.+ Iye amene amati akatsegula palibe wina amene angatseke, ndipo akatseka palibe wina amene angatsegule. 8 ‘Ndikudziwa ntchito zako.+ Taona! Ndakutsegulira khomo+ pamaso pako, limene wina sangalitseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa, ndiponso kuti unasunga mawu anga. Ndikudziwanso kuti wakhala wokhulupirika ku dzina langa.+ 9 Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama+ kuti ndi Ayuda+ pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama+ pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda. 10 Popeza unasunga mawu onena za kupirira kwanga,+ inenso ndidzakusunga+ pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakusunga pa ola limene likubwera kudzayesa okhala padziko lapansi.+ 11 Ndikubwera mofulumira.+ Gwirabe mwamphamvu chimene uli nacho,+ kuti wina asakulande mphoto* yako.+
12 “‘Wopambana pa nkhondo, ndidzamuika kukhala mzati+ m’kachisi+ wa Mulungu wanga,+ ndipo sadzachokamonso. Ndidzamulemba dzina la Mulungu wanga, ndiponso dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano,+ wotsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga. Ndidzamulembanso dzina langa latsopano.+ 13 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’
14 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena Ame,+ mboni+ yokhulupirika+ ndi yoona,+ woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.+ 15 ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha. 16 Choncho, chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha+ kapena wozizira,+ ndikulavula m’kamwa mwanga. 17 Iwe ukunena kuti: “Ndine wolemera,+ ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,” koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu,+ ndi wamaliseche. 18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone.
19 “‘Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.+ Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.+ 20 Taona! Ndaima pakhomo,+ ndipo ndikugogoda. Wina akamva mawu anga ndi kutsegula chitseko,+ ndidzalowa m’nyumba mwake ndipo iye ndi ine tidzadyera limodzi chakudya chamadzulo. 21 Wopambana pa nkhondo+ ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu,+ monga mmene ine ndinakhalira+ ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu+ nditapambana pa nkhondo. 22 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’”+
4 Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khomo lotseguka kumwamba. Ndipo mawu oyamba amene ndinawamva akundilankhula anali ngati kulira kwa lipenga.+ Mawuwo anali akuti: “Kwera kumwamba kuno,+ ndikuonetse zinthu zimene ziyenera kuchitika.”+ 2 Zitatero, nthawi yomweyo ndinakhala mumphamvu ya mzimu, ndipo mpando wachifumu+ unaoneka uli pamalo ake kumwamba,+ wina atakhalapo.+ 3 Wokhala pampandoyo, anali wooneka+ ngati mwala wa yasipi,+ ndi mwala wofiira wamtengo wapatali. Utawaleza+ wooneka ngati mwala wa emarodi+ unazungulira mpando wachifumuwo.
4 Kuzungulira mpando wachifumuwo, panalinso mipando yachifumu yokwanira 24. Pamipando yachifumuyo,+ ndinaona patakhala akulu+ 24+ ovala malaya akunja oyera,+ ndi zisoti zachifumu+ zagolide pamitu pawo. 5 Kumpando wachifumuko kunali kutuluka mphezi,+ mawu, ndi mabingu.+ Panalinso nyale+ zamoto 7 zikuyaka patsogolo pa mpando wachifumuwo. Zimenezo zikuimira mizimu 7+ ya Mulungu. 6 Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali nyanja yoyera mbee! ngati galasi,+ yooneka ngati mwala wa kulusitalo.
Pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo, ndiponso mouzungulira, panali zamoyo zinayi+ zokhala ndi maso ambirimbiri, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. 7 Chamoyo choyamba chinali ngati mkango.+ Chamoyo chachiwiri chinali ngati mwana wa ng’ombe wamphongo.+ Chamoyo+ chachitatu chinali ndi nkhope ngati ya munthu, ndipo chamoyo+ chachinayi chinali ngati chiwombankhanga+ chimene chikuuluka. 8 Zamoyo zinayizo,+ chilichonse chinali ndi mapiko 6.+ Zinali ndi maso thupi lonse ngakhalenso kunsi kwa mapiko.+ Zamoyo zimenezi sizinali kupuma usana ndi usiku. Zinali kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova+ Mulungu, Wamphamvuyonse,+ amene analipo, amene alipo,+ ndi amene akubwera.”
9 Nthawi zonse zamoyozo zikamapereka ulemerero, ndi ulemu, ndiponso zikamayamikira+ Wokhala pampando wachifumuyo,+ Iye amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya,+ 10 akulu 24 aja+ anali kugwada ndi kuwerama pamaso pa Wokhala pampando wachifumuyo, ndi kulambira+ wokhala ndi moyo kwamuyayayo. Iwo anali kuponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa mpando wachifumuwo, ndi kunena kuti: 11 “Ndinu woyenera, inu Yehova* Mulungu wathu wamphamvu,+ kulandira ulemerero+ ndi ulemu,+ chifukwa munalenga zinthu zonse,+ ndipo mwa kufuna kwanu,+ zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”+
5 Kenako, ndinaona mpukutu wolembedwa mkati ndi kunja komwe,+ uli m’dzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu.+ Unali womatidwa+ mwamphamvu ndi zidindo 7 zomatira. 2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti: “Ndani ali woyenera kumatula zidindo zimene amatira mpukutuwu ndi kuutsegula?” 3 Koma sipanapezeke ndi mmodzi yemwe, kaya kumwamba, padziko lapansi, kapena pansi pa nthaka, wotha kutsegula mpukutuwo kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga. 4 Choncho ine ndinalira kwambiri chifukwa sipanapezeke wina aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo, kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga.+ 5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pa nkhondo+ moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.”
6 Kenako ndinaona mwana wa nkhosa+ wooneka ngati wophedwa,+ ataimirira pafupi ndi mpando wachifumu+ uja ndi zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu aja.+ Iye anali ndi nyanga 7, ndi maso 7. Maso amenewo akuimira mizimu 7 ya Mulungu,+ imene yatumizidwa m’dziko lonse lapansi. 7 Iye anapita, ndipo nthawi yomweyo anatenga mpukutu umene unali kudzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu.+ 8 Atatenga mpukutuwo, zamoyo zinayi ndi akulu 24 aja+ anagwada ndi kuwerama pamaso pa Mwanawankhosa. Aliyense wa iwo anali ndi zeze woimbira+ ndi mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza. Zofukizazo+ zikuimira mapemphero+ a oyera. 9 Iwo anali kuimba nyimbo yatsopano,+ yakuti: “Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa, ndipo ndi magazi anu,+ munagula+ anthu kuti atumikire Mulungu.+ Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. 10 Ndipo munawasandutsa mafumu+ ndi ansembe+ a Mulungu wathu,+ moti adzakhala mafumu+ olamulira dziko lapansi.”
11 Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi zamoyo zija ndi akulu aja. Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda*+ ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.+ 12 Iwo anali kunena mofuula kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa+ ndiye woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero, ndi madalitso.”+
13 Ndipo cholengedwa chilichonse chakumwamba, padziko lapansi,+ pansi pa nthaka, panyanja, ndi zinthu zonse za mmenemo, ndinazimva zikunena kuti: “Iye wokhala pampando wachifumu,+ ndi Mwanawankhosa,+ atamandidwe ndiponso alandire ulemu,+ ulemerero,+ ndi mphamvu, kwamuyaya.” 14 Ndiyeno zamoyo zinayi zija zinati: “Ame!” Ndipo akulu aja+ anagwada n’kuwerama ndi kulambira.+
6 Ndinaona Mwanawankhosa+ atamatula chidindo chimodzi mwa zidindo 7 zija,+ ndipo ndinamva chamoyo chimodzi mwa zamoyo zinayi zija+ chikulankhula ndi mawu ngati kugunda kwa bingu kuti: “Bwera!”+ 2 Nditayang’ana, ndinaona hatchi* yoyera.+ Wokwerapo+ wake ananyamula uta.+ Iye anapatsidwa chisoti chachifumu,+ ndi kupita kukagonjetsa adani ake+ ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.+
3 Atamatula chidindo chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri+ chikunena kuti: “Bwera!” 4 Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.+
5 Atamatula+ chidindo chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu+ chikunena kuti: “Bwera!” Ndipo nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo+ m’dzanja lake. 6 Kenako ndinamva mawu ngati ochokera pakati+ pa zamoyo zinayi zija.+ Mawuwo anali akuti: “Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi,+ ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.”+
7 Atamatula chidindo chachinayi, ndinamva mawu a chamoyo chachinayi+ chikunena kuti: “Bwera!” 8 Nditayang’ana, ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda+ anali kumutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali,+ njala,+ mliri wakupha, ndi zilombo+ za padziko lapansi.
9 Atamatula chidindo chachisanu, ndinaona pansi pa guwa lansembe+ pali miyoyo+ ya amene anaphedwa+ chifukwa cha mawu a Mulungu, ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni+ imene anali nayo. 10 Iwo anafuula ndi mawu okweza akuti: “Mudzalekerera kufikira liti, Inu Ambuye Wamkulu Koposa,+ woyera ndi woona,+ osaweruza+ ndi kubwezera okhala padziko lapansi chifukwa cha magazi+ athu?” 11 Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera,+ ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa+ monga mmene iwonso anaphedwera.
12 Atamatula chidindo cha 6, ndinaona kuti kunachitika chivomezi chachikulu. Dzuwa linada ngati chiguduli*+ choluka ndi ubweya wa mbuzi yakuda, ndipo mwezi wonse unafiira ngati magazi.+ 13 Nyenyezi zakumwamba zinagwera kudziko lapansi, ngati mmene mkuyu wogwedezeka ndi mphepo yamphamvu umagwetsera nkhuyu zake zosapsa. 14 Ndipo kumwamba kunakanganuka ngati mpukutu umene akuupinda,+ ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa m’malo awo.+ 15 Mafumu a dziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemera, amphamvu, kapolo aliyense ndi mfulu aliyense, anabisala m’mapanga ndi m’matanthwe+ a m’mapiri. 16 Iwo anali kuuza mapiri ndi matanthwe mosalekeza kuti: “Tigwereni,+ tibiseni kuti tisaonekere kwa Iye amene wakhala pampando wachifumu,+ ndiponso kuti tibisike ku mkwiyo wa Mwanawankhosa,+ 17 chifukwa tsiku lalikulu+ la mkwiyo wawo+ lafika, ndipo ndani angaimirire pamaso pawo?”+
7 Zimenezi zitatha, ndinaona angelo+ anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi+ za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja, kapena pamtengo uliwonse.+ 2 Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,+ ali ndi chidindo cha Mulungu+ wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu, kwa angelo anayiwo, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja. 3 Anafuula kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo+ pamphumi+ za akapolo a Mulungu wathu.”
4 Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera m’fuko lililonse+ la ana a Isiraeli,+ anadindidwa chidindo:
5 Mu fuko la Yuda,+ anadindamo anthu 12,000.
Mu fuko la Rubeni,+ 12,000.
Mu fuko la Gadi,+ 12,000.
Mu fuko la Nafitali,+ 12,000.
Mu fuko la Manase,+ 12,000.
7 Mu fuko la Simiyoni,+ 12,000.
Mu fuko la Levi,+ 12,000.
Mu fuko la Isakara,+ 12,000.
8 Mu fuko la Zebuloni,+ 12,000.
Mu fuko la Yosefe,+ 12,000.
9 Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu,+ limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse,+ fuko lililonse, mtundu uliwonse,+ ndi chinenero chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu+ ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza+ m’manja mwawo. 10 Iwo anapitirizabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu,+ amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+
11 Pamenepo angelo+ onse anaimirira mozungulira mpando wachifumu, limodzi ndi akulu,+ ndi zamoyo zinayi zija.+ Ndipo onse anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu.+ 12 Iwo anali kunena kuti: “Ame! Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu+ ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.”+
13 Ndiyeno mmodzi wa akulu+ aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani, ndipo achokera kuti?” 14 Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anati: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu,+ ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa+ m’magazi+ a Mwanawankhosa. 15 N’chifukwa chake ali pamaso+ pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika+ usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo+ adzatambasulira hema+ wake pamwamba pawo kuti awateteze. 16 Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17 chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta+ ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi+ a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”+
8 Atamatula+ chidindo cha 7,+ kumwamba kunangoti chete! pafupifupi hafu ya ola. 2 Kenako ndinaona angelo 7+ ataimirira pamaso pa Mulungu, ndipo anapatsidwa malipenga 7.
3 Mngelo wina anafika ndi kuimirira kuguwa+ lansembe. Iye anali ndi chiwiya chofukiziramo chagolide, ndipo anamupatsa zofukiza zambiri+ kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide, limene linali pamaso pa mpando wachifumu. 4 Pamenepo, utsi wa zofukizazo unakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m’dzanja la mngeloyo limodzi ndi mapemphero+ a oyera. 5 Koma nthawi yomweyo, mngeloyo anatenga chiwiya chofukiziramo chija, n’kudzazamo moto+ umene anapala paguwa lansembe, ndi kuuponyera kudziko lapansi.+ Ndiyeno kunagunda mabingu,+ kunamveka mawu, ndipo kunachita mphezi+ ndi chivomezi.+ 6 Angelo 7 okhala ndi malipenga+ 7+ aja, anakonzekera kuliza malipengawo.
7 Mngelo woyamba analiza lipenga lake. Atatero, panaoneka matalala ndi moto,+ zosakanikirana ndi magazi. Zimenezi zinaponyedwa kudziko lapansi. Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi linapsa.+ Kuwonjezera pamenepo, gawo limodzi mwa magawo atatu a mitengo linapsa, komanso zomera zonse zobiriwira+ zinapsa.
8 Kenako mngelo wachiwiri analiza lipenga lake. Ndipo chinachake chokhala ngati phiri lalikulu+ limene likuyaka moto chinaponyedwa m’nyanja.+ Moti gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja, linasanduka magazi.+ 9 Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zamoyo zimene zili m’nyanja zinafa.+ Komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a ngalawa, linasweka.
10 Tsopano mngelo wachitatu analiza lipenga lake. Ndipo nyenyezi yaikulu yoyaka ngati nyale inagwa kuchokera kumwamba.+ Inagwera pa gawo limodzi mwa magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe a madzi.+ 11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chitsamba Chowawa. Choncho gawo limodzi mwa magawo atatu a madzi linakhala lowawa, ndipo anthu ambiri anafa ndi madziwo chifukwa anali owawa.+
12 Ndiyeno mngelo wachinayi analiza lipenga lake. Atatero, gawo limodzi mwa magawo atatu a dzuwa linakanthidwa. Chimodzimodzinso gawo limodzi mwa magawo atatu a mwezi, ndi a nyenyezi. Zinatero kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a zimenezi lichite mdima, ndi kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a usana+ lisalandire kuunika,+ chimodzimodzinso usiku.
13 Ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga+ chikuuluka pafupi m’mlengalenga,+ chikulankhula ndi mawu okweza kuti: “Tsoka, tsoka, tsoka+ kwa okhala padziko lapansi, chifukwa cha malipenga otsalawo, amene angelo atatuwo atsala pang’ono kuwaliza!”+
9 Kenako mngelo wachisanu analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinaona nyenyezi+ imene inagwera kudziko lapansi kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi+ wa dzenje+ lolowera kuphompho. 2 Pamene inatsegula dzenje lolowera kuphompholo, utsi+ ngati wa m’ng’anjo yaikulu+ unatuluka m’dzenjemo, ndipo dzuwa ndi mpweya zinada+ ndi utsi wa m’dzenjewo. 3 Mu utsiwo, munatuluka dzombe+ n’kubwera padziko lapansi. Dzombelo linapatsidwa ulamuliro wofanana ndi umene zinkhanira+ za padziko lapansi zili nawo. 4 Ndipo linauzidwa kuti lisawononge zomera za padziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma livulaze anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.+
5 Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze+ miyezi isanu. Ndipo kuzunzika kwawo kunali kofanana ndi mmene munthu amazunzikira akalumidwa ndi chinkhanira.+ 6 M’masiku amenewo, anthuwo adzafunafuna imfa,+ koma sadzaipeza. Adzalakalaka kufa, koma imfa izidzawathawa.
7 Dzombelo linali kuoneka ngati mahatchi+ okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali zinthu zooneka ngati zisoti zachifumu zokhala ngati zagolide. Nkhope zawo zinali ngati nkhope za amuna,+ 8 koma tsitsi lawo linali ngati la akazi.+ Mano awo anali ngati a mikango.+ 9 Pachifuwa pawo panali zotetezera+ zokhala ngati zachitsulo. Ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta+ okokedwa ndi mahatchi ambiri omwe akuthamangira kunkhondo.+ 10 Dzombelo linali ndi michira ndi mbola ngati zinkhanira.+ M’michira yawoyo ndi mmene munali ulamuliro wawo wovulaza anthuwo kwa miyezi isanu. 11 Dzombelo lili ndi mfumu. Mfumuyo ndiye mngelo wa phompho.+ M’Chiheberi, dzina lake ndi Abadoni, koma m’Chigiriki ali ndi dzina lakuti Apoliyoni.+
12 Tsoka limodzilo linapita. Koma masoka ena awiri+ anali kubwera pambuyo pa zimenezi.
13 Kenako mngelo wa 6+ analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinamva mawu amodzi+ kuchokera panyanga za paguwa lansembe lagolide+ lokhala pamaso pa Mulungu. 14 Mawuwo anauza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: “Masula angelo anayi+ omangidwa+ amene ali kumtsinje waukulu wa Firate.”+ 15 Angelo anayiwo anamasulidwa. Iwo anali okonzekera kuti pa ola, tsiku, mwezi, ndi chaka chimenecho, aphe gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.
16 Ndipo chiwerengero cha makamu a asilikali okwera pamahatchi, chinali miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda.* Chimenechi ndicho chiwerengero chawo chimene ndinamva. 17 Mahatchi ndi okwerapowo ndinawaona motere m’masomphenyawo: Anavala zoteteza pachifuwa zofiira ngati moto, zobiriwira ngati mwala wa huwakinto, ndi zachikasu ngati sulufule. Mitu ya mahatchiwo inali ngati mitu ya mikango,+ ndipo m’kamwa mwawo munali kutuluka moto, utsi, ndi sulufule.+ 18 M’kamwa mwawomo munalinso kutuluka miliri itatu iyi: Moto, utsi, ndi sulufule, ndipo inapha gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu. 19 Ulamuliro wa mahatchiwo unali m’kamwa mwawo ndi m’michira yawo, pakuti michira yawo inali ngati njoka,+ ndipo inali ndi mitu. Zinthu zimenezi anali kuwononga nazo anthu.
20 Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo.+ Sanalape kulambira ziwanda+ ndi mafano agolide, asiliva,+ amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+ 21 Iwo sanalape ntchito zawo zopha anthu,+ zamizimu,+ dama lawo, ngakhalenso umbava wawo.
10 Kenako, ndinaona mngelo+ wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba, atavala mtambo.+ Kumutu kwake kunali utawaleza, ndipo nkhope yake inali ngati dzuwa.+ Miyendo yake+ inali ngati mizati yamoto. 2 M’dzanja lake, anali ndi mpukutu waung’ono wofunyulula. Iye anaponda panyanja ndi phazi lake lamanja, koma ndi phazi lake lamanzere anaponda pamtunda.+ 3 Kenako anafuula ndi mawu okweza ngati kubangula kwa mkango.+ Atafuula choncho, mabingu 7+ analankhula, bingu lililonse ndi liwu lakelake.
4 Tsopano mabingu 7 aja atalankhula, ndinafuna kulemba. Koma ndinamva mawu kumwamba+ akuti: “Tsekera zimene+ mabingu 7 amenewo alankhula, usazilembe.” 5 Mngelo amene ndinamuona ataimirira panyanja ndi pamtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba.+ 6 Iye analumbira pa Iye wokhala+ ndi moyo kwamuyaya,+ amene analenga kumwamba ndi zokhala kumeneko, ndi dziko lapansi+ ndi zinthu za mmenemo,+ ndi nyanja ndi zinthu za mmenemo. Analumbira kuti: “Sipakhalanso kuchedwa ayi.+ 7 Koma m’masiku oliza lipenga la mngelo wa 7,+ mngeloyo atatsala pang’ono kuliza lipenga lake,+ ndithu chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu chidzathetsedwa, malinga ndi uthenga wabwino umene anaulengeza kwa akapolo ake, aneneri.”+
8 Kenako, mawu+ amene ndinawamva kuchokera kumwamba aja, analankhulanso ndi ine kuti: “Pita, katenge mpukutu wofunyulula umene uli m’dzanja la mngelo amene waimirira panyanja ndi pamtunda uja.”+ 9 Choncho, ndinapita kwa mngeloyo n’kumuuza kuti andipatse mpukutu waung’onowo. Iye anandiuza kuti: “Tenga mpukutuwu udye.+ Ukupweteketsa m’mimba, koma m’kamwa mwako ukhala wozuna ngati uchi.” 10 Chotero ndinatenga mpukutu waung’onowo m’dzanja la mngeloyo n’kuudya.+ M’kamwa mwanga, unali wozuna ngati uchi,+ koma nditaudya, unandipweteketsa m’mimba. 11 Ndiye iwo anandiuza kuti: “Uyenera kuneneranso zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu ambiri.”+
11 Ndiyeno ndinapatsidwa bango lokhala ngati ndodo+ ndipo ndinauzidwa kuti: “Nyamuka, kayeze nyumba yopatulika ya pakachisi+ wa Mulungu, guwa lansembe, ndi amene akulambira mmenemo. 2 Koma bwalo lakunja+ kwa nyumba yopatulika ya pakachisi ulisiye, usaliyeze m’pang’ono pomwe chifukwa laperekedwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo iwo adzapondaponda mzinda woyera+ kwa miyezi 42.+ 3 Ndiyeno ndidzachititsa mboni zanga ziwiri+ kunenera+ kwa masiku 1,260, zitavala ziguduli.”+ 4 Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi,+ ndi zoikapo nyale ziwiri,+ ndipo mbonizo zaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.+
5 Ngati wina aliyense akufuna kuzivulaza, moto umatuluka m’kamwa mwawo ndi kupsereza adani awo.+ Ngati wina angafune kuzivulaza, ayenera kuphedwa mwanjira imeneyi. 6 Mboni zimenezi zili ndi ulamuliro wotseka kumwamba+ kuti mvula isagwe+ m’masiku onse amene zikunenera. Zilinso ndi ulamuliro pamadzi, woti ziwasandutse magazi.+ Komanso zili ndi ulamuliro wokantha dziko lapansi ndi mliri wamtundu uliwonse, maulendo ambirimbiri mogwirizana ndi mmene zingafunire.
7 Zikamaliza kuchitira umboni wawo, chilombo chotuluka muphompho+ chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa ndi kuzipha.+ 8 Mitembo yawo idzagona pamsewu waukulu mumzinda waukulu, umene mophiphiritsira ukutchedwa Sodomu+ ndi Iguputo, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwa.+ 9 Mitundu ya anthu, mafuko, zinenero, ndi mayiko,+ adzayang’anitsitsa mitembo yawo masiku atatu ndi hafu,+ ndipo sadzalola kuti mitemboyo iikidwe m’manda. 10 Okhala padziko lapansi adzakondwera+ kwambiri ndi imfa yawoyo. Iwo adzatumizirana+ mphatso, chifukwa aneneri awiriwa anazunza okhala padziko lapansi.
11 Masiku atatu ndi hafu+ aja atatha, mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unalowa mwa mboni zija.+ Ndiyeno mbonizo zinaimirira, ndipo amene anali kuziona anagwidwa ndi mantha aakulu. 12 Kenako mbonizo zinamva mawu ofuula+ ochokera kumwamba akuziuza kuti: “Kwerani kuno.”+ Ndipo zinakwera kumwamba mumtambo, moti adani awo anaziona. 13 Mu ola limenelo, kunachitika chivomezi chachikulu, ndipo gawo limodzi mwa magawo khumi+ a mzindawo linagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomezicho, ndipo ena onse anachita mantha n’kupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba.+
14 Tsoka+ lachiwiri linapita. Koma tsoka lachitatu linali kubwera mofulumira.
15 Mngelo wa 7 analiza lipenga+ lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake.+ Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.”+
16 Ndipo akulu 24 aja,+ amene anali atakhala pamipando yawo yachifumu pamaso pa Mulungu, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo analambira Mulungu+ 17 ndi mawu akuti: “Tikukuyamikani+ inu Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse,+ Inu amene mulipo+ ndi amene munalipo, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu+ ndi kuyamba kulamulira monga mfumu.+ 18 Koma mitundu ya anthu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika. Inafikanso nthawi yoikidwiratu yakuti akufa aweruzidwe, nthawi yopereka mphoto+ kwa akapolo anu aneneri,+ ndiponso kwa oyerawo, ndi oopa dzina lanu, olemekezeka ndi onyozeka omwe.+ Komanso, nthawi yowononga+ amene akuwononga dziko lapansi.”+
19 Nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu imene ili kumwamba+ inatsegulidwa, ndipo likasa+ la pangano lake linaonekera m’nyumba yake yopatulika+ ya pakachisi. Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomezi, ndipo kunagwa matalala ambiri zedi.
12 Kenako chizindikiro chachikulu+ chinaoneka kumwamba. Ndicho mkazi+ atavala dzuwa, ndipo mwezi unali kunsi kwa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12, 2 ndipo mkaziyo anali ndi pakati. Iye analira pomva ululu+ chifukwa cha zowawa za pobereka.
3 Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu+ chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7. 4 Mchira+ wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi+ zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja,+ amene anali pafupi kubereka,+ kuti akabereka chidye+ mwana wakeyo.
5 Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.+ 6 Koma mkaziyo anathawira kuchipululu,+ kumene Mulungu anamukonzera malo, kuti akadyetsedwe+ masiku 1,260.+
7 Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, 8 koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. 9 Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija,+ iye wotchedwa Mdyerekezi+ ndi Satana,+ amene akusocheretsa dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi,+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10 Ndipo ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti:
“Tsopano chipulumutso,+ mphamvu,+ ufumu wa Mulungu wathu,+ ndi ulamuliro wa Khristu+ wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11 Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa,+ ndiponso chifukwa cha mawu a umboni wawo.+ Ndipo iwo sanaone kuti miyoyo yawo ndi yofunika,+ ngakhale pamene anali pa ngozi yoti akhoza kufa. 12 Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!+ Tsoka+ dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+
13 Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi,+ chinazunza mkazi+ amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14 Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri+ a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu,+ kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa+ kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi njoka ija.+
15 Kenako njokayo inalavula madzi+ ngati mtsinje kuchokera m’kamwa mwake, kulavulira mkazi uja, kuti amizidwe ndi mtsinjewo.+ 16 Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo.+ Dzikolo linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera m’kamwa mwake. 17 Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja,+ moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni+ za Yesu.
13 Ndiyeno chinjokacho chinangoima pamchenga+ wa m’mbali mwa nyanja.
Kenako ndinaona chilombo+ chikutuluka m’nyanja.+ Chinali ndi nyanga 10+ ndi mitu 7.+ Kunyanga yake iliyonse kunali chisoti chachifumu. Koma pamitu yake panali mayina onyoza Mulungu.+ 2 Chilombo chimene ndinaonacho chinali ngati nyalugwe,+ koma mapazi ake anali ngati a chimbalangondo,+ ndipo pakamwa pake panali ngati pa mkango.+ Chinjoka+ chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.+
3 Ndiyeno ndinaona mutu wake umodzi ukuoneka kuti wavulazidwa kwambiri. Koma ngakhale kuti balalo linali loti chikanafa nalo,+ linapola. Ndipo dziko lonse lapansi linatsatira chilombocho pochita nacho chidwi. 4 Iwo analambira chinjoka chija chifukwa chinapatsa chilombo ulamuliro. Ndipo analambira chilombocho ndi mawu awa: “Ndani ali ngati chilombo, ndipo ndani angamenyane nacho?” 5 Chilombocho chinapatsidwa pakamwa polankhula zinthu zodzitukumula+ ndi zonyoza.+ Chinapatsidwanso mphamvu yochita ulamuliro kwa miyezi 42.+ 6 Chilombocho chinatsegula pakamwa pake n’kumanyoza Mulungu,+ dzina lake ndi malo ake okhala, ndiponso amene akukhala kumwamba.+ 7 Chinaloledwa+ kuchita nkhondo ndi oyerawo ndi kuwagonjetsa.+ Chinapatsidwanso ulamuliro pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse. 8 Ndipo onse okhala padziko lapansi adzachilambira. Anthu onsewa mayina awo sanalembedwe mumpukutu+ wa moyo, umene Mwanawankhosa amene anaphedwa,+ ndiye mwiniwake. Mpukutuwo unakonzedwa kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+
9 Aliyense amene ali ndi makutu amve.+ 10 Ngati wina akuyenera kutengedwa ukapolo, adzapitadi ku ukapoloko.+ Ngati wina adzapha ndi lupanga, adzaphedwa ndi lupanga.+ Apa m’pamene oyera+ akufunika kupirira+ ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.+
11 Kenako ndinaona chilombo+ china chikutuluka pansi pa dziko lapansi.+ Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka.+ 12 Chilombocho chinalamulira ndi mphamvu zonse za chilombo choyambacho+ pamaso pa chilombo choyambacho. Chinachititsa dziko lapansi ndi okhalamo kulambira chilombo choyamba chija, chimene bala lake limene chinayenera kufa nalo, linapola.+ 13 Chinachitanso zizindikiro zazikulu,+ moti chinapangitsa ngakhale moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona.
14 Chilombocho chinasocheretsa okhala padziko lapansi chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Ndipo chinauza okhala padziko lapansi kupanga chifaniziro+ cha chilombo chimene chinali ndi bala la lupanga+ chija, koma chimene chinapulumuka. 15 Ndipo chinaloledwa kupereka mpweya ku chifaniziro cha chilombo chija, kuti chifaniziro cha chilombocho chithe kulankhula, ndi kuchititsa kuti onse amene mwa njira iliyonse salambira chifaniziro+ cha chilombocho, aphedwe.
16 Chilombocho chinakakamiza anthu onse,+ olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.+ 17 Chinachita izi kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina+ la chilombo, kapena nambala ya dzina lake.+ 18 Apa ndiye pofunika nzeru: Amene ali ndi nzeru awerengere nambala ya chilombocho, pakuti ndi nambala ya munthu.+ Nambala yake ndi 666.+
14 Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa+ ataimirira paphiri la Ziyoni.+ Limodzi naye panali enanso 144,000+ olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate+ wake pamphumi pawo. 2 Kenako ndinamva phokoso kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri,+ ndiponso ngati phokoso la bingu lamphamvu. Phokoso ndinamvalo linali ngati la oimba amene akuimba motsagana ndi azeze awo.+ 3 Iwo anali kuimba+ nyimbo yokhala ngati yatsopano+ pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa zamoyo zinayi,+ ndi pamaso pa akulu.+ Palibe anatha kuiphunzira nyimboyo, koma 144,000+ amene anagulidwa+ padziko lapansi. 4 Awa ndiwo amene sanadziipitse ndi akazi,+ ndipo ali ngati anamwali.+ Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.+ Iwowa anagulidwa+ kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira+ zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. 5 M’kamwa mwawo simunapezeke chinyengo,+ ndipo alibe chilema.+
6 Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga.+ Iye anali ndi uthenga wabwino+ wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.+ 7 Iye anali kunena mofuula kuti: “Opani Mulungu+ ndi kumupatsa ulemerero,+ chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika.+ Chotero lambirani Iye amene anapanga+ kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.”+
8 Kenako mngelo wina wachiwiri anamutsatira, ndipo anati: “Wagwa! Babulo+ Wamkulu wagwa,+ amene anachititsa mitundu yonse ya anthu kumwako vinyo+ wa mkwiyo wake ndi wa dama* lake!”+
9 Mngelo wina wachitatu anawatsatira, ndipo ananena mofuula kuti: “Ngati wina walambira chilombo+ ndi chifaniziro chake,+ ndipo walandira chizindikiro pamphumi kapena padzanja lake,+ 10 adzamwanso vinyo wosasungunula wa mkwiyo+ wa Mulungu amene akuthiridwa m’kapu ya mkwiyo wake. Ndipo adzazunzidwa+ ndi moto ndi sulufule+ pamaso pa angelo oyera, ndi pamaso pa Mwanawankhosa. 11 Ndipo utsi wa kuzunzidwa kwawo udzafuka kwamuyaya.+ Amene anali kulambira chilombo ndi chifaniziro chake, ndiponso aliyense amene walandira chizindikiro+ cha dzina lake, sadzapuma usana ndi usiku. 12 Kwa oyerawo,+ amene akusunga malamulo a Mulungu+ ndi kutsatira chikhulupiriro+ cha Yesu, apa ndiye pofunika kupirira.”
13 Kenako ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti: “Lemba: Odala ndiwo anthu amene akufa+ mwa Ambuye+ kuyambira pa nthawi ino kupita m’tsogolo.+ Mzimu ukuti, alekeni akapumule ku ntchito yawo imene anaigwira mwakhama, pakuti zimene anachita zikupita nawo limodzi.”
14 Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.
15 Mngelo wina anatuluka m’nyumba yopatulika ya pakachisi, akufuula kwa wokhala pamtambo uja ndi mawu okweza, kuti: “Tsitsa chikwakwa chako ndi kuyamba kumweta,+ chifukwa ola la kumweta lafika.+ Pakuti zokolola za padziko lapansi zapsa bwino.”+ 16 Choncho wokhala pamtambo uja anatsitsira chikwakwa chake chija kudziko lapansi mwamphamvu, ndipo anamweta dziko lapansi.
17 Mngelo winanso anatuluka m’nyumba yopatulika ya pakachisi amene ali kumwamba,+ nayenso ali ndi chikwakwa chakuthwa.
18 Ndipo mngelo winanso anatuluka kuguwa lansembe. Iyeyu anali ndi ulamuliro pa moto.+ Anafuula kwa mngelo amene anali ndi chikwakwa chakuthwa uja ndi mawu okweza, akuti: “Tsitsa chikwakwa chako chakuthwacho umwete mpesa wa padziko lapansi,+ ndi kusonkhanitsa pamodzi masango a mphesa zake, chifukwa mphesa zakezo zapsa.” 19 Mngeloyo+ anatsitsira chikwakwa chake kudziko lapansi mwamphamvu, ndi kumweta mpesa+ wa padziko lapansi. Ndiyeno anauponya m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.+ 20 Ndipo anapondaponda mopondera mphesamo kunja kwa mzinda,+ ndipo magazi anatuluka m’choponderamo mphesacho mpaka kufika m’zibwano za mahatchi,+ n’kuyenderera mtunda wa masitadiya 1,600.*+
15 Ndipo ndinaona chizindikiro china+ kumwamba, chachikulu ndi chodabwitsa. Ndicho angelo 7+ okhala ndi miliri 7.+ Imeneyi ndiyo yomaliza, chifukwa ndiyo ikumalizitsa+ mkwiyo+ wa Mulungu.
2 Kenako ndinaona chooneka ngati nyanja yagalasi+ yosakanikirana ndi moto. Ndipo amene anagonjetsa+ chilombo chija, chifaniziro chake,+ ndi nambala+ ya dzina lake, ndinawaona ataimirira pambali pa nyanja yagalasiyo,+ ali ndi azeze+ a Mulungu. 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti:
“Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+ 4 Kodi ndani sadzakuopani,+ inu Yehova?+ Ndani sadzalemekeza dzina lanu?+ Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika.+ Mitundu yonse ya anthu idzabwera kudzalambira pamaso panu,+ chifukwa malamulo anu olungama aonekera.”+
5 Zimenezi zitatha, ndinaona malo opatulika a m’chihema+ cha umboni+ atatsegulidwa kumwamba.+ 6 Ndipo angelo 7+ okhala ndi miliri 7+ aja anatuluka kumalo opatulikawo, atavala zovala zoyera+ ndi zowala, atavalanso zoteteza pachifuwa zagolide. 7 Ndiye chimodzi cha zamoyo zinayi+ zija chinapatsa angelo 7 amenewo mbale zagolide 7, zodzaza ndi mkwiyo wa Mulungu,+ amene adzakhala ndi moyo kwamuyaya.+ 8 Ndipo malo opatulikawo anadzaza utsi chifukwa cha ulemerero wa Mulungu,+ ndiponso chifukwa cha mphamvu zake. Palibe amene anatha kulowa m’malo opatulikawo, mpaka miliri 7+ ya angelo 7 aja itatha.
16 Kenako, ndinamva mawu ofuula+ ochokera m’malo opatulika akuuza angelo 7 aja kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo+ wa Mulunguzo kudziko lapansi.”
2 Mngelo woyamba+ anapita n’kukathira mbale yake padziko lapansi.+ Pamenepo mliri wa zilonda zopweteka ndi zonyeka+ unagwa pakati pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo,+ amenenso anali kulambira chifaniziro chake.+
3 Mngelo wachiwiri+ anathira mbale yake m’nyanja.+ Ndipo nyanja inasanduka magazi+ ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse m’nyanjamo chinafa.+
4 Mngelo wachitatu+ anathira mbale yake pamitsinje+ ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi.+ 5 Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: “Inu Amene mulipo ndi amene munalipo,+ inu Wokhulupirika,+ ndinu wolungama chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi,+ 6 pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri.+ Ndipo inu mwawapatsa magazi+ kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.”+ 7 Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: “Inde, Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse,+ zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.”+
8 Mngelo wachinayi+ anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutentha+ anthu ndi moto. 9 Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu,+ amene ali ndi ulamuliro+ pa miliri imeneyi, ndipo sanalape kuti amupatse ulemerero.+
10 Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo.+ Pamenepo ufumu wake unachita mdima,+ ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. 11 Koma iwo ananyoza+ Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo.
12 Mngelo wa 6+ anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate,+ ndipo madzi ake anauma,+ kuti njira ya mafumu+ ochokera kotulukira dzuwa ikonzedwe.
13 Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa,+ ooneka ngati achule,+ akutuluka m’kamwa mwa chinjoka,+ m’kamwa mwa chilombo,+ ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga.+ 14 Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwa+ ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro.+ Mauthengawo akupita kwa mafumu+ a dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo+ ya tsiku lalikulu+ la Mulungu Wamphamvuyonse.+
15 “Taona! Ndikubwera ngati mbala.+ Wodala ndi amene akhalabe maso+ ndi kukhalabe chivalire malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu n’kuona maliseche ake.”+
16 Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.*+
17 Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya.+ Atatero, kunamveka mawu ofuula+ kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” 18 Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagunda mabingu. Kunachitanso chivomezi chachikulu+ chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi,+ chivomezi+ champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. 19 Pamenepo mzinda waukulu+ unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu,+ kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu.+ 20 Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke.+ 21 Ndipo matalala aakulu,+ lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu+ chifukwa cha mliri wa matalalawo,+ pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.
17 Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7+ aja, anabwera n’kundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikulu+ lokhala pamadzi ambiri,+ 2 limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama,+ ndipo linaledzeretsa anthu okhala padziko lapansi ndi vinyo wa dama* lake.”+
3 Mu mphamvu ya mzimu,+ mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo+ chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu.+ Chinali ndi mitu 7,+ ndi nyanga 10. 4 Mkaziyo anavala zovala zofiirira+ ndi zofiira kwambiri.+ Anadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale.+ M’dzanja lake, anali ndi kapu yagolide+ yodzaza ndi zonyansa+ ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi dama lake.+ 5 Pamphumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi+ lakuti: “Babulo Wamkulu, mayi wa mahule+ ndi wa zonyansa za padziko lapansi.”+ 6 Ndipo ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi+ a oyera, ndiponso magazi a mboni za Yesu.+
Nditamuona mkaziyo, ndinadabwa kwambiri.+ 7 Koma mngelo uja anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi ameneyu,+ ndi cha chilombo chimene wakwerapo, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10:+ 8 Chilombo chimene waona, chinalipo,+ tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho,+ ndipo chidzapita ku chiwonongeko. Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri pochita nacho chidwi. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo+ kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+
9 “Apa m’pamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru:+ Mitu 7+ ikuimira mapiri 7,+ amene mkazi uja amakhala pamwamba pake. 10 Palinso mafumu 7. Asanu agwa,+ imodzi ilipo,+ inayo sinafikebe.+ Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.+ 11 Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma tsopano palibe,+ n’chimenenso chili mfumu ya 8, koma yotuluka mwa mafumu 7 aja, ndipo ikupita ku chiwonongeko.
12 “Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10+ amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi. 13 Mafumuwa maganizo awo ndi amodzi, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho.+ 14 Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa,+ koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu,+ Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.+ Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”+
15 Kenako mngeloyo anandiuza kuti: “Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.+ 16 Nyanga 10+ waziona zija, komanso chilombo,+ zimenezi zidzadana nalo hulelo.+ Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.+ 17 Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake,+ kuti zikwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo,+ kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.+ 18 Ndipo mkazi+ amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.”+
18 Zimenezi zitatha, ndinaona mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro+ waukulu. Ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero wake.+ 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+ 3 Iye wamwetsa mitundu yonse ya anthu+ vinyo wa mkwiyo, vinyo wa dama lake. Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.+ Amalonda oyendayenda+ a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.”+
4 Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga,+ ngati simukufuna kugawana naye machimo ake,+ ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake. 5 Pakuti machimo ake aunjikana mpaka kumwamba,+ ndipo Mulungu wakumbukira+ zochita zake zopanda chilungamo. 6 M’bwezereni monga mmene iye anachitira.+ M’chitireni mowirikiza kawiri. Ndithu, wirikizani kawiri zinthu zimene iyeyo anachita.+ M’kapu+ imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho+ kuwirikiza kawiri.+ 7 Pa muyezo umene anadzipezera ulemerero ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, pa muyezo womwewo mumuzunze ndi kumuliritsa.+ Pakuti mumtima mwake akumanena kuti, ‘Ine ndine mfumukazi.+ Sindine mkazi wamasiye,+ ndipo sindidzalira+ ngakhale pang’ono.’ 8 Ndiye chifukwa chake m’tsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yakeyo+ ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto+ chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu.+
9 “Mafumu+ a dziko lapansi amene anachita naye dama ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye,+ poona utsi+ wofuka chifukwa cha kupsa kwake. 10 Ndipo ataima patali poona kuzunzika kwake, adzati,+ ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe!+ Babulo iwe, mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!’+
11 “Komanso, amalonda oyendayenda+ a padziko lapansi adzamulira+ maliro ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina wowagula katundu wawo yense, 12 katundu yense+ wagolide, siliva, mwala wamtengo wapatali, ndi ngale. Komanso palibe wowagula nsalu zabwino kwambiri, zofiirira, zasilika, zofiira kwambiri, ndi mtengo uliwonse wa fungo lokoma, komanso chilichonse chopangidwa ndi mnyanga, chilichonse chopangidwa ndi mtengo wapamwamba, ndi chamkuwa, chachitsulo, ndi chamwala wa mabo.+ 13 Komanso palibe wowagula sinamoni, amomo,* zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ng’ombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo, ndi anthu.+ 14 Zoonadi, chipatso chabwino chimene moyo wako unali kulakalaka+ chakuchokera. Zinthu zako zonse zabwino ndi zokongola zawonongeka, ndipo anthu sadzazipezanso.+
15 “Amalonda oyendayenda+ a zinthu zimenezi, amene analemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona kuzunzika kwake. Iwo adzamulira maliro ndi kumva chisoni+ 16 ndipo azidzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe+ wovala zovala zapamwamba, zofiirira, ndi zofiira kwambiri. Mzinda wokongoletsedwa mochititsa kaso iwe, ndi zokongoletsera zagolide, zamwala wamtengo wapatali, ndi zangale.+ 17 Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’+
“Woyendetsa ngalawa aliyense ndi munthu aliyense woyenda panyanja kuchokera kulikonse,+ ogwira ntchito m’ngalawa ndi onse oyenda panyanja pochita malonda awo, anaima patali.+ 18 Poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake, iwo anafuula kuti, ‘Ndi mzinda uti ungafanane ndi mzinda waukulu+ umenewu?’ 19 Iwo anathira fumbi pamitu pawo+ akufuula, kulira ndi kumva chisoni,+ ndipo anati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwu, umene unalemeretsa+ onse okhala ndi ngalawa panyanja+ chifukwa cha chuma chake chamtengo wapatali, pakuti mu ola limodzi, wawonongedwa.’+
20 “Kondwerani kumwambako+ chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera,+ inu atumwi,+ ndi inu aneneri, kondwerani chifukwa Mulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.”+
21 Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala wooneka ngati mphero yaikulu+ n’kuuponya m’nyanja,+ ndipo anati: “Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso.+ 22 Pamenepo kuimba kwa oimba motsagana ndi zeze, kwa oimba zitoliro, kwa oimba malipenga, ndi kwa oimba ena, sikudzamvekanso+ mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, ngakhale phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe. 23 Kuwala kwa nyale sikudzaunikanso mwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso+ mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda+ anali anthu apamwamba+ padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.+ 24 Mwa iye munapezeka magazi+ a aneneri,+ a oyera,+ ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.”+
19 Zimenezi zitatha, ndinamva mawu ofuula kumwamba+ ngati mawu a khamu lalikulu, akuti: “Tamandani Ya,* anthu inu!+ Chipulumutso,+ ulemerero, ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,+ 2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama* lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”+ 3 Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya, anthu inu!+ Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.”+
4 Ndipo akulu+ 24 ndi zamoyo zinayi zija,+ anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhala+ pampando wachifumu, ndi mawu akuti: “Ame! Tamandani Ya,+ anthu inu!”
5 Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapolo+ ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.”+
6 Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka ngati mkokomo wa madzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: “Tamandani Ya,+ anthu inu, chifukwa Yehova* Mulungu wathu, Wamphamvuyonse,+ wayamba kulamulira monga mfumu.+ 7 Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero,+ chifukwa ukwati+ wa Mwanawankhosa wafika,+ ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.+ 8 Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”+
9 Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwa+ ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati+ wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: “Awa ndi mawu oona a Mulungu.”+ 10 Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire.+ Koma iye anandiuza kuti:+ “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ pakuti kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha maulosi.”+
11 Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo.+ 12 Maso ake anali ngati lawi la moto+ ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu+ zambiri. Anali ndi dzina+ lolembedwa limene wina aliyense sanali kulidziwa, koma iye yekha. 13 Iye anavala malaya akunja owazidwa magazi,+ ndipo dzina limene anali kutchedwa nalo linali lakuti Mawu+ a Mulungu. 14 Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! 15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse. 16 Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+
17 Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame+ zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo, 18 kuti mudzadye minofu+ ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi+ ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”
19 Ndipo ndinaona chilombo,+ mafumu+ a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane+ ndi wokwera pahatchi+ uja ndi gulu lake lankhondo. 20 Koma chilombocho+ chinagwidwa limodzi ndi mneneri+ wonyenga uja, amene anachita zizindikiro+ pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro+ cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake.+ Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.+ 21 Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi,+ limene linatuluka m’kamwa mwake lija.+ Ndipo mbalame+ zonse zinakhuta+ minofu yawo.+
20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho+ ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. 2 Kenako anagwira chinjoka,+ njoka yakale ija,+ amene ndi Mdyerekezi+ ndiponso Satana,+ ndi kumumanga zaka 1,000. 3 Ndipo anamuponyera m’phompho+ ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.+
4 Kenako ndinaona mipando yachifumu+ ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza.+ Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo+ kapena chifaniziro chake,+ ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu+ limodzi ndi Khristu zaka 1,000. 5 (Akufa+ enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.)+ Uku ndi kuuka koyamba+ kwa akufa. 6 Wodala+ ndi woyera+ ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.+
7 Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa m’ndende yake, 8 ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja.+ 9 Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera,+ ndi mzinda wokondedwa.+ Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza.+ 10 Mdyerekezi,+ amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo+ ndi mneneri wonyenga uja.+ Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya.
11 Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo.+ Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa+ pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. 12 Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka,+ ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo.+ Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+ 13 Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa+ amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.+ 14 Ndipo imfa+ ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto.+ Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.+ 15 Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo+ anaponyedwa m’nyanja yamoto.+
21 Tsopano ndinaona kumwamba+ kwatsopano ndi dziko lapansi+ latsopano, pakuti kumwamba+ kwakale ndi dziko lapansi lakale+ zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja.+ 2 Ndinaonanso mzinda woyera,+ Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba+ kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi+ wokongoletsedwera mwamuna wake.+ 3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+ 4 Iye adzapukuta misozi+ yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira,+ kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”+
5 Ndipo wokhala pampando wachifumu+ anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”+ Ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.” 6 Anandiuzanso kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.+ Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.+ 7 Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake,+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ 8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+
9 Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri+ 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”+ 10 Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali,+ ndipo anandionetsa mzinda woyera,+ Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu,+ 11 uli ndi ulemerero wa Mulungu.+ Unali wonyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.+ 12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali,+ ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli.+ 13 Kum’mawa kwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu.+ 14 Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko+ yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12+ a Mwanawankhosa.
15 Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango+ lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake.+ 16 Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo+ ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana. 17 Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144,* malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo. 18 Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi,+ ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 19 Maziko+ a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse:+ maziko oyamba anali amwala wa yasipi,+ achiwiri wa safiro,+ achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi,+ 20 achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito,+ a 8 wa belulo, a 9 wa topazi,+ a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito.*+ 21 Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi.+ Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.
22 Sindinaone kachisi mumzindawo,+ pakuti Yehova+ Mulungu Wamphamvuyonse+ ndiye anali kachisi+ wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake.+ 23 Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa,+ ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.+ 24 Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake,+ ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo.+ 25 Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana,+ ndipo usiku sudzakhalako.+ 26 Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.+ 27 Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa+ ndiponso wabodza,+ sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.+
22 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo,+ oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.+ 2 Mtsinjewo unali kudutsa pakati pa msewu waukulu wa mumzindawo. Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo+ ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse.+ Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.+
3 Sikudzakhalanso temberero.+ Koma mpando wachifumu wa Mulungu+ ndi wa Mwanawankhosa+ udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulika+ kwa iye. 4 Iwo adzaona nkhope yake,+ ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo.+ 5 Komanso, usiku sudzakhalakonso.+ Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova Mulungu adzawaunikira.+ Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.+
6 Kenako anandiuza kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona.+ Yehova, Mulungu wopereka mauthenga ouziridwa+ a aneneri,+ anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa.+ 7 Ndipo taonani! Ndikubwera mofulumira.+ Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi a mumpukutu uwu.”+
8 Ine Yohane, ndine amene ndinali kumva ndi kuona zinthu zimenezi. Ndipo nditamva ndi kuona, ndinagwada n’kuwerama kuti ndilambire+ pamapazi a mngelo amene anali kundionetsa zinthu zimenezi. 9 Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ndiwo aneneri,+ ndi wa anthu amene akusunga mawu a mumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.”+
10 Anandiuzanso kuti: “Usatsekere mawu a ulosi a mumpukutu uwu, pakuti nthawi yoikidwiratu yayandikira.+ 11 Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama,+ ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo.+ Koma wolungama+ achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.+
12 “‘Taonani! Ndikubwera mofulumira,+ ndipo mphoto+ ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake.+ 13 Ine ndine Alefa ndi Omega,+ woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto.+ 14 Odala ndiwo amene achapa mikanjo+ yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo,+ ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake.+ 15 Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu,+ amene amachita zamizimu,+ adama,+ opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.’+
16 “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+
17 Mzimu+ ndi mkwatibwi+ akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!”+ Aliyense wakumva ludzu abwere.+ Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.+
18 “Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense wakumva mawu a ulosi wa mumpukutuwu, kuti: Wina akawonjezera+ pa zimenezi, Mulungu adzamuwonjezera miliri+ yolembedwa mumpukutuwu. 19 Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo,+ ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo.+
20 “Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’”+
“Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.”
21 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo.+
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 5.
Kapena kuti, “amithenga.”
Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Onani Zakumapeto 7.
“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.
Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Onani Zakumapeto 2.
Kapena kuti, “10,000 kuchulukitsa ndi ma 10,000.”
Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Ena amati “saka.”
Kapena kuti, “20,000 kuchulukitsa ndi 10,000,” imene ndi 200 miliyoni. Onani mawu a m’munsi pa Chv 5:11.
Onani Zakumapeto 7.
Makilomita 296. “Sitadiya” ndi muyezo wakale wachigiriki woyezera mtunda. “Sitadiya” imodzi ndi yofanana ndi mamita 185.
Kapena kuti, “Aramagedo.” M’Chiheberi, mawuwa akutanthauza, “Phiri la Megido.”
Onani Zakumapeto 7.
Kapena kuti, “zonunkhiritsa zochokera ku India.”
Kapena kuti, “Aleluya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Onani Zakumapeto 7.
Onani Zakumapeto 2.
Makilomita pafupifupi 2,200. Onani mawu a m’munsi pa Chv 14:20.
Mamita pafupifupi 64.
Yonseyi ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yosiyanasiyana, ndipo ina ndi yokhala ndi mitundu ingapo yosiyana m’mwala umodzi.