Mbiri Woyamba
5 Ana a Yafeti anali Gomeri, Magogi,+ Madai,+ Yavani,+ Tubala, Meseke,+ ndi Tirasi.+
6 Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati,+ ndi Togarima.+
7 Ana a Yavani anali Elisaha,+ Tarisi,+ Kitimu,+ ndi Rodanimu.+
8 Ana a Hamu anali Kusi,+ Miziraimu,+ Puti,+ ndi Kanani.+
9 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita,+ Raama,+ ndi Sabiteka.+
Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.+
10 Kusi anabereka Nimurodi+ amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.+
11 Miziraimu anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 12 Patirusimu,+ ndi Kasiluhimu+ (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu), ndiponso Kafitorimu.+
13 Kanani anabereka Sidoni+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 14 Anaberekanso Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi,+ 15 Ahivi,+ Aariki, Asini,+ 16 Aarivadi,+ Azemari,+ ndi Ahamati.+
18 Aripakisadi anabereka Shela,+ ndipo Shela anabereka Ebere.+
19 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa m’masiku ake, dziko lapansi linagawikana. M’bale wakeyo dzina lake anali Yokitani.
20 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 21 Hadoramu, Uzali, Dikila,+ 22 Obali, Abimaele, Sheba,+ 23 Ofiri,+ Havila,+ ndi Yobabi.+ Onsewa anali ana a Yokitani.
28 Ana a Abulahamu anali Isaki+ ndi Isimaeli.+
29 Awa ndiwo mabanja awo: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 30 Misima, Duma,+ Maasa, Hadadi,+ Tema, 31 Yeturi, Nafisi, ndi Kedema.+ Amenewa ndiwo anali ana a Isimaeli.
32 Ketura+ mdzakazi*+ wa Abulahamu anabereka Zimirani, Yokesani, Medani,+ Midiyani,+ Isibaki,+ ndi Shuwa.+
Ana a Yokesani anali Sheba ndi Dedani.+
33 Ana a Midiyani anali Efa,+ Eferi, Hanoki, Abida, ndi Elida.+
Onsewa anali ana aamuna a Ketura.
34 Abulahamu anabereka Isaki.+ Ana a Isaki anali Esau+ ndi Isiraeli.+
35 Ana a Esau anali Elifazi, Reueli,+ Yeusi, Yalamu, ndi Kora.+
36 Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu, Kenazi,+ Timina,+ ndi Amaleki.+
37 Ana a Reueli anali Nahati, Zera, Shama, ndi Miza.+
38 Ana a Seiri+ anali Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,+ Disoni, Ezeri, ndi Disani.+
39 Ana a Lotani anali Hori ndi Homamu. Mlongo wake wa Lotani anali Timina.+
40 Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo, ndi Onamu.+
Ana a Zibeoni anali Aya ndi Ana.+
41 Mwana* wa Ana anali Disoni.+
Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani, ndi Kerana.+
42 Ana a Ezeri+ anali Bilihani, Zavani, ndi Ekani.+
Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+
43 Tsopano awa ndiwo mafumu amene analamulira dziko la Edomu+ ana a Isiraeli asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse:+ Bela mwana wa Beori. Dzina la mzinda wake linali Dinihaba.+ 44 Patapita nthawi, Bela anamwalira ndipo Yobabi mwana wa Zera+ wa ku Bozira,+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 45 Patapita nthawi, Yobabi anamwalira ndipo Husamu+ wa kudziko la Atemani,+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 46 Patapita nthawi, Husamu anamwalira ndipo Hadadi+ mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani+ m’dziko la Mowabu, anayamba kulamulira m’malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Aviti.+ 47 Patapita nthawi, Hadadi anamwalira ndipo Samila wa ku Masereka+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 48 Patapita nthawi, Samila anamwalira ndipo Shauli wa ku Rehoboti+ mzinda wa m’mphepete mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira m’malo mwake. 49 Patapita nthawi, Shauli anamwalira ndipo Baala-hanani mwana wa Akibori+ anayamba kulamulira m’malo mwake. 50 Patapita nthawi, Baala-hanani anamwalira ndipo Hadadi anayamba kulamulira m’malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau, ndipo mkazi wake dzina lake linali Mehetabele mwana wa Matiredi mwana wamkazi wa Mezahabu.+ 51 Patapita nthawi, Hadadi anamwalira.
Mafumu a Edomu anali mfumu Timina, mfumu Aliva, mfumu Yeteti,+ 52 mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni,+ 53 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari,+ 54 mfumu Magidieli, ndi mfumu Iramu.+ Amenewa ndiwo anali mafumu+ a Edomu.
2 Awa ndiwo anali ana a Isiraeli:+ Rubeni,+ Simiyoni,+ Levi,+ Yuda,+ Isakara,+ Zebuloni,+ 2 Dani,+ Yosefe,+ Benjamini,+ Nafitali,+ Gadi,+ ndi Aseri.+
3 Ana a Yuda anali Ere,+ Onani,+ ndi Shela.+ Mwana wamkazi wa Sua Mkanani ndiye anam’berekera ana atatuwa. Ere mwana woyamba wa Yuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo iye anamupha.+ 4 Tamara+ mpongozi wake ndiye anam’berekera Perezi+ ndi Zera. Ana onse a Yuda anali asanu.
5 Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+
6 Ana a Zera+ anali Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli, ndi Dara.+ Onse pamodzi analipo asanu.
7 Mwana wa Karami+ anali Akari,* amene anachititsa Isiraeli kunyanyalidwa.+ Iye anachita zinthu zosakhulupirika zokhudzana ndi chinthu choyenera kuwonongedwa.+
8 Mwana wa Etani+ anali Azariya.
9 Ana amene Hezironi+ anabereka anali Yerameeli,+ Ramu,+ ndi Kelubai.
10 Ramu anabereka Aminadabu, Aminadabu+ anabereka Naasoni+ mtsogoleri wa ana a Yuda. 11 Naasoni anabereka Salima,+ Salima anabereka Boazi,+ 12 Boazi anabereka Obedi,+ Obedi anabereka Jese,+ 13 Jese anabereka mwana wake woyamba Eliyabu,+ wachiwiri Abinadabu,+ wachitatu Simeya,+ 14 wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15 wa 6 Ozemu, ndipo wa 7 anali Davide.+ 16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli,+ ndipo Zeruya anali ndi ana atatu: Abisai,+ Yowabu,+ ndi Asaheli.+ 17 Abigayeli anabereka Amasa,+ ndipo bambo ake a Amasa anali Yeteri+ Mwisimaeli.
18 Kalebe mwana wa Hezironi+ anabereka ana kudzera mwa Azuba mkazi wake ndiponso kudzera mwa Yerioti. Ana akewo anali: Yeseri, Sobabu, ndi Aridoni. 19 Patapita nthawi, Azuba anamwalira. Chotero Kalebe anakwatira Efurata,+ yemwe m’kupita kwa nthawi anam’berekera Hura.+ 20 Hura anabereka Uri.+ Uri anabereka Bezaleli.+
21 Kenako Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri,+ bambo wa Giliyadi.+ Hezironi anakwatira ali ndi zaka 60, koma mkaziyo anam’berekera Segubu. 22 Segubu anabereka Yairi,+ amene anadzakhala ndi mizinda 23+ m’dziko la Giliyadi. 23 Kenako Gesuri+ ndi Siriya+ analanda Havoti-yairi.+ Analandanso Kenati+ ndi midzi yake yozungulira, mizinda 60. Onsewa anali ana a Makiri, bambo wa Giliyadi.
24 Hezironi+ atamwalira ku Kalebe-efurata, Abiya mkazi wake anam’berekera Ashari bambo wa Tekowa.+
25 Ana a Yerameeli+ mwana woyamba wa Hezironi anali Ramu+ woyamba kubadwa, ndi Buna, Oreni, Ozemu, ndi Ahiya. 26 Yerameeli anakwatira mkazi wina dzina lake Atara. Iye anali mayi ake a Onamu. 27 Ana a Ramu+ mwana woyamba wa Yerameeli anali Maazi, Yamini, ndi Ekeri. 28 Ana a Onamu+ anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri. 29 Mkazi wa Abisuri dzina lake linali Abihaili, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’berekera Abani ndi Molidi. 30 Ana a Nadabu+ anali Seledi ndi Apaimu, koma Seledi anamwalira wopanda mwana. 31 Mwana wa Apaimu anali Isi, mwana wa Isi anali Sesani,+ mwana wa Sesani anali Alai. 32 Ana a Yada m’bale wake wa Samai anali Yeteri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda mwana. 33 Ana a Yonatani anali Pelete ndi Zaza. Awa ndiwo anali ana a Yerameeli.
34 Sesani+ analibe ana aamuna, koma anali ndi ana aakazi. Iye anali ndi wantchito wachiiguputo+ dzina lake Yaha. 35 Choncho Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yaha kuti akhale mkazi wake, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’berekera Atai. 36 Atai anabereka Natani, Natani anabereka Zabadi,+ 37 Zabadi anabereka Efilali, Efilali anabereka Obedi, 38 Obedi anabereka Yehu, Yehu anabereka Azariya, 39 Azariya anabereka Helezi, Helezi anabereka Eleasa, 40 Eleasa anabereka Sisimai, Sisimai anabereka Salumu, 41 Salumu anabereka Yekamiya, ndipo Yekamiya anabereka Elisama.
42 Ana a Kalebe+ m’bale wake wa Yerameeli anali Mesa mwana wake woyamba, yemwe anali bambo wa Zifi, ndi ana a Maresha bambo wa Heburoni. 43 Ana a Heburoni anali Kora, Tapuwa, Rekemu, ndi Sema. 44 Sema anabereka Rahamu bambo wa Yorikeamu. Rekemu anabereka Samai. 45 Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali bambo wa Beti-zuri.+ 46 Efa mdzakazi wa Kalebe anabereka Harana, Moza, ndi Gazezi. Harana anabereka Gazezi. 47 Ana a Yahadai anali Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa, ndi Safa. 48 Maaka mdzakazi wa Kalebe anabereka Seberi ndi Tirana. 49 M’kupita kwa nthawi anabereka Safa bambo wa Madimana.+ Anaberekanso Seva bambo wa Makibena ndi Gibeya.+ Mwana wamkazi wa Kalebe+ anali Akisa.+ 50 Awa ndiwo anali ana a Kalebe.
Tsopano awa ndiwo ana a Hura+ mwana woyamba wa Efurata:+ Sobala+ bambo wa Kiriyati-yearimu,+ 51 Salima bambo wa Betelehemu,+ ndi Harefi bambo wa Beti-gaderi. 52 Sobala+ bambo wa Kiriyati-yearimu anabereka ana awa: Haroye, ndi hafu ya anthu otchedwa Amenuhoti. 53 Mabanja a Kiriyati-yearimu anali Aitiri,+ Aputi, Asumati, ndi Amisirai. Azorati+ ndi Aesitaoli+ anachokera ku mabanja amenewa. 54 Ana a Salima anali anthu okhala ku Betelehemu,+ ku Netofa,+ ndi ku Atiroti-beti-yowabu. Hafu ya anthu okhala ku Manahati ndi anthu okhala ku Zora, analinso ana a Salima. 55 Mabanja a alembi amene anali kukhala ku Yabezi+ anali Atirati, Asimeati, ndi Asukati. Amenewa anali Akeni+ amene anachokera kwa Hamati bambo wa nyumba ya Rekabu.+
3 Ana amene Davide+ anabereka ku Heburoni+ anali awa: woyamba Aminoni,+ wobadwa kwa Ahinowamu+ wa ku Yezereeli,+ wachiwiri Danieli, wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli,+ 2 wachitatu Abisalomu,+ wobadwa kwa Maaka+ mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya Gesuri,+ wachinayi Adoniya,+ wobadwa kwa Hagiti,+ 3 wachisanu Sefatiya, wobadwa kwa Abitali,+ wa 6 Itireamu, wobadwa kwa Egila+ mkazi wake. 4 Davide anabereka ana 6 ku Heburoni ndipo analamulira kumeneko zaka 7 ndi miyezi 6. Kenako analamulira zaka 33 ku Yerusalemu.+
5 Ku Yerusalemu+ iye anabereka ana awa: Simeya,+ Sobabu,+ Natani,+ ndi Solomo,+ ana anayi obadwa kwa Bati-seba+ mwana wamkazi wa Amiyeli.+ 6 Anaberekanso Ibara,+ Elisama,+ Elifeleti,+ 7 Noga, Nefegi, Yafiya,+ 8 Elisama,+ Eliyada, ndi Elifeleti,+ ana 9. 9 Amenewa ndiwo anali ana onse a Davide, kuwonjezera pa ana a adzakazi ake, ndipo Tamara+ anali mlongo wawo.
10 Mwana wa Solomo anali Rehobowamu.+ Rehobowamu anabereka Abiya,+ Abiya anabereka Asa,+ Asa anabereka Yehosafati,+ 11 Yehosafati anabereka Yehoramu,+ Yehoramu anabereka Ahaziya,+ Ahaziya anabereka Yehoasi,+ 12 Yehoasi anabereka Amaziya,+ Amaziya anabereka Azariya,+ Azariya anabereka Yotamu,+ 13 Yotamu anabereka Ahazi,+ Ahazi anabereka Hezekiya,+ Hezekiya anabereka Manase,+ 14 Manase anabereka Amoni,+ ndipo Amoni anabereka Yosiya.+ 15 Ana a Yosiya anali awa: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu,+ wachitatu Zedekiya,+ ndipo wachinayi anali Salumu. 16 Mwana wa Yehoyakimu anali Yekoniya.+ Yekoniya anabereka Zedekiya. 17 Ana amene Yekoniya anabereka ali mkaidi anali Salatiyeli,+ 18 Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama, ndi Nedabiya. 19 Ana a Pedaya anali Zerubabele+ ndi Simeyi. Ana a Zerubabele anali Mesulamu ndi Hananiya, (Selomiti anali mlongo wawo), 20 Hasuba, Oheli, Berekiya, Hasadiya, ndi Yusabi-hesedi, ana asanu. 21 Ana a Hananiya anali Pelatiya+ ndi Yesaiya, mwana wa Yesaiya anali Refaya, mwana wa Refaya anali Arinani, mwana wa Arinani anali Obadiya, mwana wa Obadiya anali Sekaniya, 22 mwana wa Sekaniya anali Semaya, ndipo ana a Semaya anali Hatusi, Igali, Bariya, Neariya, ndi Safati, ana 6. 23 Ana a Neariya anali Elioenai, Hizikiya, ndi Azirikamu, ana atatu. 24 Ana a Elioenai anali Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya, ndi Anani, ana 7.
4 Ana a Yuda anali Perezi,+ Hezironi,+ Karami,+ Hura,+ ndi Sobala.+ 2 Reyaya+ mwana wa Sobala anabereka Yahati. Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Amenewa ndiwo anali mabanja a Azorati.+ 3 Tsopano awa ndiwo ana a bambo wa Etami:+ Yezereeli,+ Isima, Idibasi, (dzina la mlongo wawo linali Hazeleleponi,) 4 Penueli bambo wa Gedori,+ ndi Ezeri bambo wa Husa. Amenewa ndiwo anali ana a Hura+ mwana woyamba wa Efurata, ndipo Hura anali bambo wa Betelehemu.+ 5 Ashari+ bambo wa Tekowa+ anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara. 6 M’kupita kwa nthawi Naara anam’berekera Ahuzamu, Heferi, Temeni, ndi Hahasitari. Amenewa ndiwo anali ana a Naara. 7 Ana a Hela anali Zereti, Izara, ndi Etani. 8 Kozi anabereka Anubu, Zobeba, ndi mabanja a Ahaheli mwana wa Harumu.
9 Yabezi+ anali wolemekezeka kwambiri+ kuposa abale ake, ndipo mayi ake ndiwo anamutcha Yabezi,* chifukwa anati: “Ndam’bereka ndikumva ululu.”+ 10 Tsopano Yabezi anayamba kuitana Mulungu+ wa Isiraeli, kuti: “Mukandidalitsa+ ndi kukulitsa dziko langa,+ ndipo dzanja lanu+ likakhala nane, komanso mukanditeteza ku tsoka,+ kuti lisandivulaze,+ . . .” Choncho Mulungu anakwaniritsa zimene iye anapempha.+
11 Kelubu m’bale wake wa Suha anabereka Mehiri, yemwe anali bambo wa Esitoni. 12 Esitoni anabereka Beti-rafa, Paseya, ndi Tehina bambo wa Iri-nahasi. Amenewa anali amuna a ku Reka. 13 Ana a Kenazi+ anali Otiniyeli+ ndi Seraya, ndipo mwana wa Otiniyeli anali Hatati. 14 Meyonatai anabereka Ofira. Seraya anabereka Yowabu bambo wa Ge-harasimu,* chifukwa iwo anakhala amisiri.+
15 Ana a Kalebe+ mwana wa Yefune+ anali Iru, Ela, ndi Naamu. Mwana wa Ela anali Kenazi. 16 Ana a Yehaleleli anali Zifi, Zifa, Tiriya, ndi Asareli. 17 Ana a Ezira anali Yeteri, Meredi, Eferi, ndi Yaloni. Mkaziyo anabereka Miriamu, Samai, ndi Isiba bambo wa Esitemowa.+ 18 Mkazi wake wachiyuda anabereka Yeredi bambo wa Gedori, Hiberi bambo wa Soko, ndi Yekutieli bambo wa Zanowa. Amenewa anali ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anam’kwatira.
19 Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, anali bambo wa Keila+ Mgarimi, ndi Esitemowa Mmaakati. 20 Ana a Shimoni anali Aminoni, Rina, Beni-hanani, ndi Tiloni. Ana a Isi anali Zoheti ndi Beni-zoheti.
21 Ana a Shela+ mwana wa Yuda anali Ere bambo wa Leka, Laada bambo wa Maresha, ndi mabanja a nyumba ya anthu ogwira ntchito yopanga nsalu zabwino kwambiri,+ a nyumba ya Asibeya, 22 Yokimu, amuna a ku Kozeba, Yowasi, ndi Sarafa, (amenewa anakwatira akazi achimowabu),+ ndi Yasubi-lehemu. Nkhani zimenezi zachokera m’zolembedwa zakale.+ 23 Iwo anali oumba zinthu+ okhala ku Netaimu ndi ku Gedera. Ankakhala kumeneko n’kumagwirira ntchito mfumu.+
24 Ana a Simiyoni anali Nemueli,+ Yamini,+ Yaribi, Zera, ndi Shauli.+ 25 Shauli anabereka Salumu, Salumu anabereka Mibisamu, Mibisamu anabereka Misima, 26 Misima anabereka Hamueli, Hamueli anabereka Zakuri, Zakuri anabereka Simeyi. 27 Simeyi anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake analibe ana ambiri. Palibe banja lawo lililonse limene linali ndi ana ambiri ngati mabanja a ana a Yuda.+ 28 Iwo anapitiriza kukhala ku Beere-seba,+ ku Molada,+ ku Hazara-suali,+ 29 ku Biliha,+ ku Ezemu,+ ku Toladi,+ 30 ku Betuele,+ ku Horima,+ ku Zikilaga,+ 31 ku Beti-marikaboti, ku Hazara-susimu,+ ku Beti-biri, ndi ku Saaraimu.+ Imeneyi inali mizinda yawo kufikira pamene Davide anayamba kulamulira.
32 Midzi yawo inali Etami, Aini, Rimoni, Tokeni, ndi Asani.+ Mizinda isanu. 33 Midzi yawo yonse yozungulira mizinda imeneyi inakafika mpaka ku Baala.+ Awa anali malo awo okhala ndi mndandanda wa mayina awo wotsatira makolo. 34 Ana ena a Simiyoni anali: Mesobabu, Yameleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35 Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, Yosibiya mwana wa Seraya, Seraya mwana wa Asieli, 36 Elioenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37 Ziza mwana wa Sifi, Sifi mwana wa Aloni, Aloni mwana wa Yedaya, Yedaya mwana wa Simuri, ndi Simuri mwana wa Semaya. 38 Amene atchulidwa mayinawa anali atsogoleri pamabanja awo,+ ndipo banja la makolo awo linakula kwambiri. 39 Iwo anapita kuchipata cha mzinda wa Gedori mpaka kukafika kum’mawa kwa chigwa, kukafuna msipu wa ziweto zawo. 40 Pomaliza pake anapeza msipu wabwino kwambiri,+ ndipo dzikolo linali lalikulu. Linali pa mtendere, lopanda chosokoneza chilichonse,+ chifukwa anthu amene ankakhala kumeneko kale anali mbadwa za Hamu.+ 41 Anthu otchulidwa mayinawa anapita kumeneko m’masiku a Hezekiya+ mfumu ya Yuda n’kukagwetsa+ mahema a Ahamu, n’kupha Ameyuni amene anali kumeneko. Anawawononga+ anthuwo, ndipo iwo kulibe mpaka lero. Kenako iwo anayamba kukhala kumeneko m’malo mwawo, chifukwa kunali msipu+ wa ziweto zawo.
42 Pakati pawo panali ana ena a Simiyoni, amuna okwana 500, amene anapita kuphiri la Seiri.+ Atsogoleri awo anali Pelatiya, Neariya, Refaya, ndi Uziyeli ana a Isi. 43 Iwo anapha Aamaleki+ otsala omwe anathawa, ndipo akukhala kumeneko mpaka lero.
5 Mwana woyamba wa Isiraeli anali Rubeni.+ Iye anali woyamba kubadwa+ koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo wake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo. 2 Chifukwa chakuti Yuda+ anali wamphamvu pakati pa abale ake, mwa iye munachokera mtsogoleri,+ koma udindo wa woyamba kubadwa unali wa Yosefe.+ 3 Ana a Rubeni mwana woyamba wa Isiraeli, anali: Hanoki,+ Palu,+ Hezironi, ndi Karami.+ 4 Mwana wa Yoweli anali Semaya. Semaya anabereka Gogi, Gogi anabereka Simeyi, 5 Simeyi anabereka Mika, Mika anabereka Reyaya, Reyaya anabereka Baala, 6 Baala anabereka Beeraha yemwe Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri inam’tenga kupita naye ku ukapolo. Iye anali mtsogoleri wa Arubeni. 7 Abale ake potsata mabanja awo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ anali Yeyeli yemwe anali mtsogoleri, Zekariya, 8 ndi Bela. Bela anali mwana wa Azazi, Azazi anali mwana wa Sema, Sema anali mwana wa Yoweli.+ Bela anali kukhala m’dera loyambira ku Aroweli+ mpaka kukafika ku Nebo+ ndi ku Baala-meoni.+ 9 Dera lake linakafika mpaka kum’mawa pamalo olowera m’chipululu pamtsinje wa Firate,+ chifukwa ziweto zawo zinachuluka kwambiri m’dziko la Giliyadi.+ 10 M’masiku a Sauli, iwo anachita nkhondo ndi Ahagara+ n’kuwagonjetsa. Kenako anayamba kukhala m’mahema awo m’dera lonse lakum’mawa kwa Giliyadi.
11 Ana a Gadi+ omwe anali pafupi nawo, anali kukhala m’dziko la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12 Mtsogoleri wawo anali Yoweli, wachiwiri wake anali Safamu. Panalinso Yanai ndi Safati ku Basana. 13 Abale awo a nyumba ya makolo awo analipo 7 ndipo amenewo anali Mikayeli, Mesulamu, Sheba, Yorai, Yakani, Ziya, ndi Ebere. 14 Amenewa anali ana a Abihaili. Abihaili anali mwana wa Huri, Huri anali mwana wa Yarowa, Yarowa anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Yesisai, Yesisai anali mwana wa Yado, Yado anali mwana wa Buza. 15 Panalinso Ahi mwana wa Abidieli, mwana wa Guni, yemwe anali mtsogoleri wa nyumba ya makolo awo. 16 Iwo anapitiriza kukhala ku Giliyadi,+ ku Basana,+ ndi m’midzi yake yozungulira+ komanso m’malo onse odyetsera ziweto a ku Sharoni, mpaka kumapeto kwa malo amenewa. 17 Onsewa analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo, m’masiku a Yotamu+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu*+ mfumu ya Isiraeli.
18 Ana a Rubeni, Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase amene anali amuna amphamvu,+ onyamula chishango ndi lupanga, odziwa kupinda uta, ndi odziwa kumenya nkhondo, analipo asilikali 44,760.+ 19 Iwo anayamba kumenyana ndi Ahagara,+ Yeturi,+ Nafisi,+ ndi Nodabu. 20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+ 21 Iwo analanda ziweto zawo.+ Analanda ngamila 50,000, nkhosa 250,000, abulu 2,000, ndipo anatenganso anthu 100,000.+ 22 Amene anafa analipo ambiri chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu woona.+ Iwo anapitiriza kukhala m’malo a anthuwo kufikira nthawi imene anatengedwa kupita kudziko lina.+
23 Ana a hafu ya fuko la Manase+ anakhala m’dera loyambira ku Basana+ mpaka ku Baala-herimoni,+ ku Seniri,+ ndi kuphiri la Herimoni,+ ndipo iwo anachulukana kwambiri. 24 Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo awo: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya, ndi Yahadieli. Onsewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, amuna amphamvu, olimba mtima, ndiponso otchuka. 25 Iwo anayamba kuchita zinthu zosakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo, ndipo anayamba kuchita chiwerewere+ ndi milungu+ ya anthu a m’dzikolo, amene Mulungu anawachotsa pamaso pawo. 26 Choncho, Mulungu wa Isiraeli analimbikitsa mtima+ wa Puli+ mfumu ya Asuri,+ ndithu analimbikitsa mtima wa Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri, moti anatenga+ Arubeni, Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase n’kuwapititsa ku Hala,+ ku Habori, ku Hara, ndi kumtsinje wa Gozani, ndipo akukhalabe kumeneko mpaka lero.
6 Ana a Levi+ anali Gerisoni,+ Kohati,+ ndi Merari.+ 2 Ana a Kohati anali Amuramu,+ Izara,+ Heburoni,+ ndi Uziyeli.+ 3 Ana a Amuramu+ anali Aroni,+ Mose,+ ndi Miriamu.+ Ana a Aroni anali Nadabu,+ Abihu,+ Eleazara,+ ndi Itamara.+ 4 Eleazara+ anabereka Pinihasi,+ Pinihasi anabereka Abisuwa,+ 5 Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi,+ 6 Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,+ 7 Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+ 8 Ahitubu anabereka Zadoki,+ Zadoki anabereka Ahimazi,+ 9 Ahimazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani, 10 ndipo Yohanani anabereka Azariya.+ Iye ndiye anali wansembe m’nyumba imene Solomo anamanga ku Yerusalemu.
11 Azariya anabereka Amariya,+ Amariya anabereka Ahitubu,+ 12 Ahitubu anabereka Zadoki, Zadoki+ anabereka Salumu, 13 Salumu anabereka Hilikiya,+ Hilikiya anabereka Azariya, 14 Azariya anabereka Seraya,+ ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.+ 15 Yehozadaki ndiye anapita ku ukapolo pamene Yehova anatengera Yuda ndi Yerusalemu ku ukapolo kudzera mwa Nebukadinezara.
16 Ana a Levi+ anali Gerisomu, Kohati, ndi Merari. 17 Ana a Gerisomu mayina awo anali Libini+ ndi Simeyi.+ 18 Ana a Kohati+ anali Amuramu,+ Izara, Heburoni, ndi Uziyeli.+ 19 Ana a Merari anali Mali ndi Musi.+
Mabanja a Alevi potsatira mayina a makolo awo ndi awa:+ 20 Mwana wa Gerisomu anali Libini,+ mwana wa Libini anali Yahati, mwana wa Yahati anali Zima, 21 mwana wa Zima anali Yowa,+ mwana wa Yowa anali Ido, mwana wa Ido anali Zera, ndipo mwana wa Zera anali Yeaterai. 22 Mwana wa Kohati anali Aminadabu, mwana wa Aminadabu anali Kora,+ ana a Kora anali Asiri, 23 Elikana, ndi Ebiasafu.+ Mwana wa Ebiasafu anali Asiri, 24 mwana wa Asiri anali Tahati, mwana wa Tahati anali Uriyeli, mwana wa Uriyeli anali Uziya, ndipo mwana wa Uziya anali Shauli. 25 Ana a Elikana+ anali Amasai ndi Ahimoti. 26 Mwana wa Elikana anali Zofai,+ mwana wa Zofai anali Nahati, 27 mwana wa Nahati anali Eliyabu,+ mwana wa Eliyabu anali Yerohamu, ndipo mwana wa Yerohamu anali Elikana.+ 28 Ana a Samueli+ anali awa: woyamba Yoweli, wachiwiri Abiya.+ 29 Mwana wa Merari anali Mali,+ mwana wa Mali anali Libini, mwana wa Libini anali Simeyi, mwana wa Simeyi anali Uza, 30 mwana wa Uza anali Simeya, mwana wa Simeya anali Hagiya, mwana wa Hagiya anali Asaya.
31 Nawa anthu amene Davide+ anawapatsa udindo wotsogolera kuimba panyumba ya Yehova ataikapo Likasa.+ 32 Anthuwa anali ndi udindo+ woyang’anira oimba+ pachihema chopatulika kapena kuti chihema chokumanako, mpaka pamene Solomo anamanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.+ Iwo anapitiriza kutumikira malinga ndi ntchito yawo.+ 33 Awa ndiwo anali kutumikira, komanso ana awo: Pa ana a Akohati, Hemani+ woimba, mwana wa Yoweli.+ Yoweli anali mwana wa Samueli,+ 34 Samueli anali mwana wa Elikana,+ Elikana anali mwana wa Yerohamu, Yerohamu anali mwana wa Elieli,+ Elieli anali mwana wa Towa, 35 Towa anali mwana wa Zufi,+ Zufi anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Mahati, Mahati anali mwana wa Amasai, 36 Amasai anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Yoweli, Yoweli anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Zefaniya, 37 Zefaniya anali mwana wa Tahati, Tahati anali mwana wa Asiri, Asiri anali mwana wa Ebiasafu,+ Ebiasafu anali mwana wa Kora,+ 38 Kora anali mwana wa Izara,+ Izara anali mwana wa Kohati, Kohati anali mwana wa Levi, Levi anali mwana wa Isiraeli.
39 M’bale wake Asafu+ anali kutumikira mbali ya kumanja kwake. Asafu anali mwana wa Berekiya,+ Berekiya anali mwana wa Simeya, 40 Simeya anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Baaseya, Baaseya anali mwana wa Malikiya, 41 Malikiya anali mwana wa Etini, Etini anali mwana wa Zera, Zera anali mwana wa Adaya, 42 Adaya anali mwana wa Etani, Etani anali mwana wa Zima, Zima anali mwana wa Simeyi, 43 Simeyi anali mwana wa Yahati,+ Yahati anali mwana wa Gerisomu,+ Gerisomu anali mwana wa Levi.
44 Pa ana a Merari,+ abale awo amene anali kumanzere kwawo, panali Etani+ mwana wa Kisa.+ Kisa anali mwana wa Abidi, Abidi anali mwana wa Maluki, 45 Maluki anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Amaziya, Amaziya anali mwana wa Hilikiya, 46 Hilikiya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Bani, Bani anali mwana wa Semeri, 47 Semeri anali mwana wa Mali, Mali anali mwana wa Musi,+ Musi anali mwana wa Merari,+ Merari anali mwana wa Levi.
48 Abale awo Alevi+ ndiwo anapatsidwa utumiki wonse+ wa pachihema chopatulika, chimene chili nyumba ya Mulungu woona. 49 Aroni+ ndi ana ake anali kufukiza nsembe yautsi+ paguwa lansembe zopsereza+ ndi paguwa lansembe zofukiza+ kuti akwaniritse ntchito zonse zokhudzana ndi zinthu zopatulika kwambiri, ndiponso kuti aphimbe machimo+ a Aisiraeli,+ malinga ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula. 50 Tsopano awa ndiwo ana a Aroni:+ Aroni anabereka Eleazara,+ Eleazara anabereka Pinihasi,+ Pinihasi anabereka Abisuwa,+ 51 Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi, Uzi anabereka Zerahiya,+ 52 Zerahiya anabereka Merayoti,+ Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+ 53 Ahitubu anabereka Zadoki,+ ndipo Zadoki anabereka Ahimazi.+
54 Otsatirawa ndiwo malo amene ankakhala ana a Aroni a m’banja la Akohati,+ m’misasa yawo yokhala ndi mipanda m’madera awo,+ chifukwa maere anagwera iwowo: 55 anapatsidwa mzinda wa Heburoni+ m’dziko la Yuda, ndi malo ake odyetserako ziweto kuzungulira mzinda wonsewo. 56 Malo ozungulira mzindawo ndi midzi yake,+ anawapereka kwa Kalebe+ mwana wa Yefune.+ 57 Ana a Aroni anawapatsa mzinda* wothawirako+ wa Heburoni,+ mzinda wa Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Yatiri,+ mzinda wa Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 58 mzinda wa Hileni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 59 mzinda wa Asani+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Beti-semesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 60 Kuchokera ku fuko la Benjamini, anawapatsa mzinda wa Geba+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Alemeti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Mizinda yonse ya mabanja awo inalipo 13.+
61 Ana a Kohati amene anatsala anawapatsa mizinda yochokera ku banja la fuko lina ndi hafu ya fuko la Manase, atachita maere. Anawapatsa mizinda 10.+
62 Ana a Gerisomu+ potsata mabanja awo anapatsidwa mizinda kuchokera ku fuko la Isakara,+ fuko la Aseri,+ fuko la Nafitali,+ ndi fuko la Manase+ ku Basana. Anapatsidwa mizinda 13.
63 Ana a Merari+ potsata mabanja awo anapatsidwa mizinda kuchokera ku fuko la Rubeni,+ fuko la Gadi,+ ndi fuko la Zebuloni.+ Anapatsidwa mizinda 12 atachita maere.
64 Chotero ana a Isiraeli anapatsa Alevi+ mizindayo ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 65 Komanso, atachita maere anawapatsa mizinda imeneyi kuchokera ku fuko la ana a Yuda,+ fuko la ana a Simiyoni,+ ndi fuko la ana a Benjamini.+ Mizindayo anachita kuitchula mayina.
66 Mabanja ena a ana a Kohati anapatsidwa mizinda m’dera lawo kuchokera ku fuko la Efuraimu.+ 67 Chotero anawapatsa mzinda wothawirako wa Sekemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto m’dera lamapiri la Efuraimu, mzinda wa Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 68 mzinda wa Yokimeamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 69 mzinda wa Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Gati-rimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 70 Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anapatsa mabanja a ana a Kohati amene anatsala,+ mzinda wa Aneri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Bileamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto.
71 Kuchokera ku banja la hafu ya fuko la Manase, anapatsa ana a Gerisomu+ mzinda wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Asitaroti+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 72 Kuchokera ku fuko la Isakara, anawapatsa mzinda wa Kedesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 73 mzinda wa Ramoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Anemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 74 Kuchokera ku fuko la Aseri anawapatsa mzinda wa Masala ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Abidoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 75 mzinda wa Hukoki+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 76 Kuchokera ku fuko la Nafitali+ anawapatsa mzinda wa Kedesi+ ku Galileya+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Hamoni ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Kiriyataimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto.
77 Kuchokera ku fuko la Zebuloni,+ anapatsa ana a Merari amene anatsala, mzinda wa Rimono+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Tabori ndi malo ake odyetserako ziweto. 78 Kuchokera ku fuko la Rubeni,+ anawapatsa mzinda wa Bezeri+ m’chipululu ndi malo ake odyetserako ziweto. Mzindawo unali m’chigawo cha Yorodano pafupi ndi Yeriko chakum’mawa kwa Yorodano. Anawapatsanso mzinda wa Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 79 mzinda wa Kademoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Mefaata+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 80 Kuchokera ku fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 81 mzinda wa Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso mzinda wa Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto.
7 Ana a Isakara analipo anayi: Tola,+ Puwa,+ Yasubi, ndi Simironi.+ 2 Ana a Tola anali Uzi, Refaya, Yerieli, Yahamai, Ibisamu, ndi Semuyeli. Amenewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo. Pa mbadwa za Tola panali amuna amphamvu ndi olimba mtima. M’masiku a Davide,+ amunawa analipo 22,600. 3 Mwana wa Uzi anali Izirahiya. Ana a Izirahiya anali Mikayeli, Obadiya, Yoweli, Isiya, ndi [?]* Anawo analipo asanu ndipo onsewa anali atsogoleri a mabanja awo. 4 Pa mibadwo ya amenewa, motsatira nyumba ya makolo awo, panali asilikali 36,000, chifukwa anali ndi akazi ndi ana ambiri.+ 5 Abale awo a mabanja onse a Isakara, anali amuna amphamvu ndi olimba mtima+ okwana 87,000 pamndandanda wa mayina awo onse wotsatira makolo awo.+
6 Ana a Benjamini+ analipo atatu: Bela,+ Bekeri,+ ndi Yediyaeli.+ 7 Ana a Bela+ analipo asanu: Eziboni, Uzi, Uziyeli, Yerimoti, ndi Iri. Iwo anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, amuna amphamvu ndi olimba mtima, ndipo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ analipo 22,034. 8 Ana a Bekeri anali Zemira, Yowasi, Eliezere, Elioenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. 9 Pamndandanda wa mayina a atsogoleri a nyumba ya makolo awo, malinga ndi mibadwo yawo,+ panali amuna amphamvu ndi olimba mtima okwanira 20,200. 10 Mwana wa Yediyaeli+ anali Bilihani. Ana a Bilihani anali Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisi, ndi Ahisahara. 11 Onsewa anali ana a Yediyaeli, atsogoleri a nyumba ya makolo awo. Anali amuna 17,200, amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ opita ku nkhondo.
12 Mabanja a Supimu+ ndi Hupimu+ anali mbadwa za Iro,+ ndipo ana a Husimu anali mbadwa za Aheri.
13 Ana a Nafitali+ anali Yazieli,+ Guni,+ Yezera, ndi Salumu,+ ana a Biliha.+
14 Mwana wa Manase+ yemwe mdzakazi wake wachisiriya anam’berekera, anali Asiriyeli. (Mdzakaziyo anabereka Makiri,+ bambo wa Giliyadi. 15 Makiri anapezera akazi Hupimu ndi Supimu, ndipo dzina la mlongo wake linali Maaka.) Mwana wake wachiwiri dzina lake linali Tselofekadi,+ koma Tselofekadi anali ndi ana aakazi okhaokha.+ 16 Patapita nthawi, Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina loti Peresi. M’bale wake wa Peresi dzina lake linali Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rekemu. 17 Mwana wa Ulamu anali Bedani. Amenewa anali ana a Giliyadi. Giliyadi anali mwana wa Makiri, ndipo Makiri anali mwana wa Manase. 18 Mlongo wake wa Giliyadi anali Hamoleketi. Iye anabereka Isihodi, Abi-ezeri,+ ndi Mala. 19 Ana a Semida anali Ahiyani, Sekemu, Liki, ndi Aniamu.
20 Mwana wa Efuraimu+ anali Sutela.+ Sutela anabereka Beredi, Beredi anabereka Tahati, Tahati anabereka Eleada, Eleada anabereka Tahati, 21 Tahati anabereka Zabadi, ndipo Zabadi anabereka Sutela. Efuraimu anaberekanso Ezeri ndi Eleadi. Iwo anaphedwa ndi amuna a ku Gati+ amene anabadwira m’dzikolo, chifukwa anabwera kudzalanda ziweto zawo. 22 Bambo wawo Efuraimu anawalira kwa masiku ambiri,+ ndipo abale ake ankabwera kudzam’tonthoza. 23 Kenako Efuraimu anagona ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo anatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna. Koma Efuraimu anatcha mwanayo dzina lakuti Beriya,* chifukwa mkaziyo anabereka pa nthawi imene tsoka+ linagwera nyumba ya Efuraimu. 24 Mwana wake wamkazi anali Seera, ndipo iye anamanga mzinda wa Beti-horoni,+ wakumunsi+ ndi wakumtunda.+ Anamanganso mzinda wa Uzeni-seera. 25 Efuraimu anabereka Refa ndi Resefe.* Resefe anabereka Tela, Tela anabereka Tahani, 26 Tahani anabereka Ladani, Ladani anabereka Amihudi, Amihudi anabereka Elisama, 27 Elisama anabereka Nuni,+ ndipo Nuni anabereka Yehoswa.*+
28 Cholowa chawo ndiponso malo awo okhala anali Beteli+ ndi midzi yake yozungulira. Kum’mawa kunali Naarani,+ kumadzulo kunali Gezeri+ ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Sekemu+ ndi midzi yake yozungulira, mpaka kukafika ku Gaza ndi midzi yake yozungulira. 29 Pafupi ndi ana a Manase panali Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, Megido+ ndi midzi yake yozungulira, ndiponso Dori+ ndi midzi yake yozungulira. Ana a Yosefe+ mwana wa Isiraeli ankakhala m’mizinda imeneyi.
30 Ana a Aseri+ anali Imuna,+ Isiva, Isivi,+ ndi Beriya,+ ndipo mlongo wawo anali Sera. 31 Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli, yemwe anali bambo wa Birizaiti. 32 Hiberi anabereka Yafuleti, Someri,* Hotamu, ndi Sua mlongo wawo. 33 Ana a Yafuleti anali Pasaki, Bimali, ndi Asivati. Amenewa anali ana a Yafuleti. 34 Ana a Semeri anali Ahi, Roga, Yehuba, ndi Aramu. 35 Ana a m’bale wake Helemu anali Zofa, Imina, Selesi, ndi Amali. 36 Ana a Zofa anali Suya, Harineferi, Suwali, Beri, Imura, 37 Bezeri, Hodi, Samima, Silisa, Itirani, ndi Beera. 38 Ana a Yeteri anali Yefune, Pisipa, ndi Era. 39 Ana a Ula anali Ara, Hanieli, ndi Riziya. 40 Onsewa anali ana a Aseri, atsogoleri+ a nyumba ya makolo awo, amuna ochita kusankhidwa, amphamvu ndi olimba mtima.+ Iwo anali akuluakulu a atsogoleri, ndipo mndandanda wa mayina awo+ anaugwiritsa ntchito powalemba usilikali, pokonzekera nkhondo. Analipo amuna 26,000.+
8 Benjamini+ anabereka Bela+ mwana wake woyamba, wachiwiri anali Asibeli,+ wachitatu anali Ahara,+ 2 wachinayi anali Noha,+ ndipo wachisanu anali Rafa. 3 Ana a Bela anali Adara, Gera,+ Abihudi, 4 Abisuwa, Namani, Ahowa, 5 Gera, Sefufani,+ ndi Huramu.+ 6 Panalinso ana a Ehudi amene anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Geba.+ Iwowa anagwira anthu ndi kuwatengera ku Manahati. 7 Atsogoleriwo anali Namani, Ahiya, ndi Gera. Gera ndiye anatengera anthuwo ku ukapolo, ndipo iye anabereka Uziza ndi Ahihudi. 8 Saharaimu anabereka ana m’dziko+ la Mowabu atathamangitsako Amowabu. Akazi ake anali Husimu ndi Baara. 9 Kwa Hodesi mkazi wake, anabereka Yobabi, Zibia, Mesa, Malikamu, 10 Yeuzi, Sakiya, ndi Mirima. Amenewa anali ana ake, atsogoleri a nyumba za makolo awo.
11 Kwa Husimu anabereka Abitubu ndi Elipaala. 12 Ana a Elipaala anali Ebere, Misamu, ndi Semedi. Semedi ndiye anamanga mzinda wa Ono+ ndiponso mzinda wa Lodi,+ ndi midzi yake yozungulira. 13 Elipaala anaberekanso Beriya ndi Sema. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Aijaloni.+ Iwo ndiwo anathamangitsa anthu a ku Gati. 14 Panalinso Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, 15 Zebadiya, Aradi, Ederi, 16 Mikayeli, Isipa, ndi Yoha. Amenewa anali ana a Beriya.+ 17 Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Hiberi, 18 Isimerai, Iziliya, ndi Yobabi anali ana a Elipaala. 19 Yakimu, Zikiri, Zabidi, 20 Elianai, Ziletai, Elieli, 21 Adaya, Beraya, ndi Simirati, anali ana a Simeyi.+ 22 Isipani, Ebere, Elieli, 23 Abidoni, Zikiri, Hanani, 24 Hananiya, Elamu, Antotiya, 25 Ifideya, ndi Penueli, anali ana a Sasaki. 26 Samuserai, Sehariya, Ataliya, 27 Yaaresiya, Eliya, ndi Zikiri, anali ana a Yerohamu. 28 Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo motsatira mzere wa mabanja awo. Iwowa ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu.+
29 Yeyeli bambo wa Gibeoni+ anali kukhala ku Gibeoni, ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka.+ 30 Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nadabu,+ 31 Gedori, Ahiyo, ndi Zekeri.+ 32 Mikiloti anabereka Simeya.+ Amenewa ndiwo anali kukhala ku Yerusalemu pamodzi ndi abale awo ena, moyang’anizana ndi abale awo.
33 Nera+ anabereka Kisi,+ Kisi anabereka Sauli,+ Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu,+ ndi Esibaala.+ 34 Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala,+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+ 35 Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tarea,+ ndi Ahazi. 36 Ahazi anabereka Yehoada. Yehoada anabereka Alemeti, Azimaveti, ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza. 37 Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Rafa,+ Rafa anabereka Eleasa, ndipo Eleasa anabereka Azeli. 38 Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali, Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya, ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli. 39 Ana a m’bale wake Ezeki anali awa: woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi, wachitatu Elifeleti. 40 Ana a Ulamu anali amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ amuna odziwa kupinda uta.+ Iwo anali ndi ana ambiri+ ndiponso zidzukulu zambiri. Onse analipo 150. Onsewa anali ana a Benjamini.
9 Aisiraeli onse analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo+ m’Buku la Mafumu a Isiraeli. Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo+ ku Babulo chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. 2 Oyamba kubwerera n’kukakhala ku cholowa chawo m’mizinda yawo anali Aisiraeli,+ ansembe,+ Alevi,+ ndi Anetini.+ 3 Ku Yerusalemu+ kunkakhala ana ena a Yuda,+ Benjamini,+ Efuraimu ndi Manase. 4 Pa anawo panali Utai mwana wa Amihudi. Amihudi anali mwana wa Omuri, Omuri anali mwana wa Imiri, ndipo Imiri anali mwana wa Bani. Amenewa anali mbadwa za Perezi+ mwana wa Yuda.+ 5 Pa anthu otchedwa Asilo,+ panali Asaya woyamba kubadwa ndiponso ana ake. 6 Pa ana a Zera+ panali Yeweli. Panalinso abale ake a Zera okwana 690.
7 Pa ana a Benjamini panali Salelu mwana wa Mesulamu. Mesulamu anali mwana wa Hodaviya, ndipo Hodaviya anali mwana wa Hasenuwa. 8 Panalinso Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi. Uzi anali mwana wa Mikiri. Panalinso Mesulamu mwana wa Sefatiya. Sefatiya anali mwana wa Reueli, ndipo Reueli anali mwana wa Ibiniya. 9 Abale awo potsatira mibadwo yawo analipo 956. Onsewa anali amuna amene anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo.
10 Pa ansembe panali Yedaya, Yehoyaribu, Yakini,+ 11 ndi Azariya+ mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Merayoti, ndipo Merayoti anali mwana wa Ahitubu. Ahitubu anali mtsogoleri wa nyumba ya Mulungu woona. 12 Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu. Yerohamu anali mwana wa Pasuri, ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya. Komanso panali Maasai mwana wa Adieli. Adieli anali mwana wa Yahazera, Yahazera anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Mesilemiti,+ ndipo Mesilemiti anali mwana wa Imeri. 13 Panalinso abale awo. Onse anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo analipo 1,760. Iwo anali amuna amphamvu, omwe anali kugwira ntchito+ yotumikira panyumba ya Mulungu woona.
14 Pa Alevi panali Semaya mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, ndipo Azirikamu anali mwana wa Hasabiya.+ Amenewa anali ochokera kwa ana a Merari. 15 Panalinso Bakabakara, Heresi, Galali, ndi Mataniya+ mwana wa Mika.+ Mika anali mwana wa Zikiri,+ ndipo Zikiri anali mwana wa Asafu.+ 16 Komanso panali Obadiya mwana wa Semaya.+ Semaya anali mwana wa Galali, Galali anali mwana wa Yedutuni.+ Ndiye panalinso Berekiya mwana wa Asa mwana wa Elikana, amene anali kukhala m’midzi ya Anetofa.+
17 Alonda a pazipata+ anali Salumu,+ Akubu, Talimoni, ndi Ahimani. Salumu m’bale wawo ndiye anali mtsogoleri. 18 Kufikira nthawi imeneyo, iye anali kukhala pachipata cha mfumu+ kum’mawa. Amenewa anali alonda a pazipata za misasa ya ana a Levi.+ 19 Panalinso Salumu mwana wa Kore. Kore anali mwana wa Ebiasafu+ ndipo Ebiasafu anali mwana+ wa Kora.+ Salumu ndi abale ake a nyumba ya makolo ake, Akora,+ anali oyang’anira ntchito pochita utumiki wawo pamodzi ndi makolo awo, monga alonda+ a pachihema pamsasa wa Yehova. Iwo anali alonda a pachipata. 20 Pinihasi+ mwana wa Eleazara+ ndiye anali mtsogoleri wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.+ 21 Zekariya+ mwana wa Meselemiya anali mlonda wa pachipata cholowera kuchihema chokumanako.
22 Onse amene anasankhidwa kuti akhale alonda a pamakomo analipo 212. Iwo anakhala m’midzi yawo+ mogwirizana ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.+ Davide+ ndi Samueli wamasomphenya+ anaika amenewa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo.+ 23 Iwo ndi ana awo anali kuyang’anira zipata za nyumba ya Yehova, kapena kuti chihema chopatulika,* ndipo ankachita utumiki waulonda.+ 24 Alonda a pazipatawo anali kukhala mbali zonse zinayi, kum’mawa,+ kumadzulo,+ kumpoto,+ ndi kum’mwera.+ 25 Abale awo amene anali kukhala m’midzi yawo, ankabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito limodzi nawo kwa masiku 7.+ 26 Pa alonda a pazipatawo panali amuna anayi amphamvu amene anali pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Amunawo anali Alevi, ndipo anali kuyang’anira zipinda zodyera+ ndi chuma+ cha m’nyumba ya Mulungu woona. 27 Usiku anali kukhala mozungulira nyumba yonse ya Mulungu woona chifukwa anali pa utumiki wawo waulonda.+ Iwo ndiwo anali kusunga kiyi kuti azitsegula zipata m’mawa uliwonse.+
28 Ena a iwo anali oyang’anira ziwiya+ za utumiki, chifukwa anali kuziwerenga pozitulutsa ndi pozilowetsa. 29 Ena a iwo anali amuna osankhidwa kuti aziyang’anira ziwiya zina, ziwiya zonse zopatulika,+ ufa wosalala,+ vinyo,+ mafuta,+ lubani,*+ ndi mafuta a basamu.+ 30 Ena mwa ana a ansembe anali opanga mafuta onunkhira+ osakaniza ndi mafuta a basamu. 31 Matitiya Mlevi, yemwe anali mwana woyamba wa Salumu+ Mkora, anali ndi udindo woyang’anira zinthu zophikidwa m’ziwaya,+ umene anapatsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake. 32 Ena mwa ana a Akohati, abale awo, anali oyang’anira mikate yosanjikiza,+ kuti aziikonza sabata ndi sabata.+
33 Amenewa ndiwo anali oimba,+ atsogoleri a makolo a Alevi m’zipinda zodyera.+ Iwo sanali kupatsidwa ntchito zina+ chifukwa usana ndi usiku anali ndi udindo wogwira ntchito yawo.+ 34 Amenewa anali atsogoleri a Alevi potsata mibadwo yawo. Iwo ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu.+
35 Yeyeli bambo wa Gibeoni+ anali kukhala ku Gibeoni, ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka. 36 Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nera, Nadabu, 37 Gedori, Ahiyo, Zekariya,+ ndi Mikiloti. 38 Mikiloti anabereka Simeamu. Amenewa ndi amene anali kukhala ku Yerusalemu pamodzi ndi abale awo ena, moyang’anizana ndi abale awo. 39 Nera+ anabereka Kisi,+ Kisi anabereka Sauli,+ Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu,+ ndi Esibaala.+ 40 Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala,+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+ 41 Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tareya, ndi Ahazi.+ 42 Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti, ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza. 43 Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Refaya,+ Refaya anabereka Eleasa, ndipo Eleasa anabereka Azeli. 44 Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya, ndi Hanani. Amenewa anali ana a Azeli.+
10 Tsopano Afilisiti+ anayamba kumenyana ndi Aisiraeli ndipo amuna a Isiraeli anali kuthawa pamaso pa Afilisitiwo, moti anali kuphedwa m’phiri la Giliboa.+ 2 Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani,+ Abinadabu+ ndi Malikisuwa,+ ana a Sauli.+ 3 Nkhondo inamukulira kwambiri Sauli, moti pamapeto pake oponya mivi ndi uta anamupeza n’kumuvulaza.+ 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida+ kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundizunza.”+ Koma womunyamulira zida uja sanafune+ kuchita zimenezo, chifukwa anali kuchita mantha kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake n’kuligwera.+ 5 Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa, nayenso anagwera palupanga n’kufa.+ 6 Chotero Sauli ndi ana ake atatu anafa,+ ndipo anthu onse a m’nyumba yake anafera limodzi. 7 Amuna onse a Isiraeli amene anali m’chigwa ataona kuti asilikaliwo athawa, komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuchoka m’mizinda yawo ndi kuthawa.+ Kenako Afilisiti anabwera n’kuyamba kukhala m’mizindayo.
8 Ndiyeno tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzavula zovala+ anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+ 9 Iwo anam’vula Sauli n’kumudula mutu,+ ndi kumuvula zida zake. Kenako anatumiza uthenga+ m’dziko lonse la Afilisiti, kwa mafano awo+ ndi kwa anthu awo. 10 Pamapeto pake, anakaika zida zakezo m’nyumba ya mulungu wawo,+ ndipo mutu wake anakaumangirira kunyumba ya Dagoni.+
11 Anthu onse a ku Yabesi+ ku Giliyadi anamva zonse zimene Afilisiti anamuchita Sauli.+ 12 Chotero amuna onse olimba mtima ananyamuka n’kukanyamula mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake n’kupita nayo ku Yabesi. Atatero anakafotsera mafupa awo pansi pa mtengo waukulu+ ku Yabesiko.+ Kenako anasala kudya+ masiku 7.
13 Choncho Sauli anafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake popeza anachita zosakhulupirika+ kwa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu.+ 14 Sauli sanafunse kwa Yehova,+ chotero iye anamupha n’kupereka ufumuwo kwa Davide mwana wa Jese.+
11 Patapita nthawi, Aisiraeli+ onse anasonkhana kwa Davide ku Heburoni+ ndi kumuuza kuti: “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.+ 2 Kuyambira kale, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inuyo munali kutsogolera Isiraeli polowa ndi potuluka.+ Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuuzani kuti, ‘Udzaweta+ anthu anga Aisiraeli, ndipo udzakhala mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli.’” 3 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Davide anachita nawo pangano ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli, mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa Samueli.+
4 Pambuyo pake Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Yerusalemu,+ kapena kuti ku Yebusi,+ dziko limene kunali kukhala Ayebusi.+ 5 Anthu okhala ku Yebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno.”+ Ngakhale zinali choncho, Davide analanda Ziyoni,+ malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, umene ndi Mzinda wa Davide.+ 6 Chotero Davide anati: “Aliyense amene ayambirire kuukira+ Ayebusi akhala mtsogoleri ndiponso kalonga.” Pamenepo Yowabu+ mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, choncho anakhala mtsogoleri. 7 Ndiyeno Davide anayamba kukhala m’malo ovuta kufikako.+ N’chifukwa chake mzindawo anautcha kuti Mzinda wa Davide.+ 8 Kenako Davide anayamba kumanga mzinda pamalo onsewo, kuyambira ku Chimulu cha Dothi* mpaka kumadera ozungulira, koma Yowabu ndiye anadzamanganso+ mzinda wonsewo. 9 Chotero ulamuliro wa Davide unakulirakulira,+ chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.+
10 Tsopano otsatirawa ndiwo atsogoleri a amuna amphamvu+ a Davide omwe anali kulimbikitsa nawo ufumu wake mwamphamvu pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu malinga ndi mawu a Yehova+ okhudza Isiraeli. 11 Uwu ndiwo mndandanda wa amuna amphamvu a Davide: Yasobeamu+ mwana wa Mhakimoni, yemwe anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 300 ulendo umodzi.+ 12 Wotsatira wake anali Eleazara+ mwana wa Dodo, Muahohi.+ Iye anali mmodzi wa amuna atatu amphamvuwo.+ 13 Iye ndiye anali limodzi ndi Davide ku Pasi-damimu+ kumene Afilisiti anasonkhana kuti achite nawo nkhondo. Kumeneko kunali munda wodzaza ndi balere, ndipo anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo.+ 14 Koma iye anaima pakati pa mundawo n’kuulanditsa. Anapha Afilisiti moti Yehova anapereka chipulumutso+ chachikulu.+
15 Kenako, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuthanthwe, kuphanga la Adulamu.+ Pa nthawiyi gulu lankhondo la Afilisiti linali litamanga msasa m’chigwa cha Arefai.+ 16 Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali a Afilisiti+ uli ku Betelehemu. 17 Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka, kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa+ madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu+ chimene chili pachipata!” 18 Pamenepo amuna atatu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+ 19 Iye anati: “Sindingachite zimenezo chifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi+ a anthuwa omwe anaika moyo wawo pachiswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.” Chotero iye anakana kumwa madziwo.+ Izi n’zimene amuna atatu amphamvu aja anachita.
20 Abisai+ m’bale wake wa Yowabu+ anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye ananyamula mkondo n’kupha anthu 300 ulendo umodzi, ndipo anali wotchuka ngati amuna atatu aja. 21 Pa amuna atatuwo, iye anali wolemekezeka kwambiri kuposa awiri enawo, ndipo anakhala mtsogoleri wawo. Koma sanafanane+ ndi amuna atatu oyambirira aja.
22 Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa. 23 Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa, yemwe anali chiphona chachitali mikono* isanu.+ Mwiguputoyo anali ndi mkondo+ m’manja mwake, waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu, koma Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+ 24 Izi n’zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita, ndipo dzina lake linali pakati pa amuna atatu amphamvu. 25 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kuposa amuna 30 aja, iye sanafikepo pa amuna atatu oyamba aja.+ Komabe Davide anamuika kukhala mtsogoleri wa asilikali omulondera.+
26 Amuna amphamvu a magulu ankhondo anali Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu, Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, 27 Samoti+ Mharori, Helezi Mpeloni,+ 28 Ira+ mwana wa Ikesi Mtekowa, Abi-ezeri Muanatoti,+ 29 Sibekai+ Mhusati, Ilai Muahohi,+ 30 Maharai+ Mnetofa,+ Heledi+ mwana wa Bana Mnetofa, 31 Ifai mwana wa Ribai+ wa ku Gibeya+ wa fuko la ana a Benjamini,+ Benaya Mpiratoni,+ 32 Hurai wa kuzigwa* za Gaasi,+ Abiyeli Muaraba, 33 Azimaveti M’bahurimu,+ Eliyaba Msaaliboni, 34 ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani+ mwana wa Sage Mharari, 35 Ahiyamu mwana wa Sakari+ Mharari, Elifali+ mwana wa Uri, 36 Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni, 37 Heziro wa ku Karimeli,+ Naarai mwana wa Ezibai, 38 Yoweli m’bale wake wa Natani,+ Mibari mwana wa Hagiri, 39 Zeleki Muamoni, Naharai M’beeroti yemwe anali wonyamula zida wa Yowabu mwana wa Zeruya, 40 Ira Muitiri, Garebi+ Muitiri, 41 Uriya+ Mhiti,+ Zabadi mwana wa Alai, 42 Adina mwana wa Siza Mrubeni yemwe anali mtsogoleri wa Arubeni okwanira 30, 43 Hanani mwana wa Maaka, Yosafati Mmitini, 44 Uzia Muasitaroti, Sama ndi Yeyeli ana a Hotamu Muaroweli, 45 Yediyaeli mwana wa Simuri, m’bale wake Yoha Mtizi, 46 Elieli Mmahavi, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu, 47 Elieli, Obedi, ndi Yaasiyeli Mmezobai.
12 Tsopano nawa anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga,+ pa nthawi imene iye sanali kuyenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa amuna amphamvu+ amene anamuthandiza pankhondo. 2 Amuna onyamula mauta amenewa, ankatha kugwiritsa ntchito mkono wamanja ndi wamanzere+ kuponyera miyala+ kapena kuponyera mivi+ pa uta.+ Amenewa anali abale ake a Sauli wa fuko la Benjamini. 3 Panali Ahiyezeri mtsogoleri wawo ndiponso Yowasi. Amenewa anali ana a Semaa wa ku Gibeya.+ Panalinso Yezieli ndi Peleti, ana a Azimaveti,+ Beraka ndi Yehu wa ku Anatoti,+ 4 Isimaya wa ku Gibeoni,+ mwamuna wamphamvu pa amuna 30+ komanso mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Kenako panali Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,+ 5 Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harifi. 6 Komanso panali Elikana, Isiya, Azareli, Yoezeri, ndi Yasobeamu. Amenewa anali mbadwa za Kora.+ 7 Panalinso Yoela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.
8 Ndiyeno panali Agadi ena amene anasankha kupita kumbali ya Davide m’chipululu,+ kumalo ovuta kufikako. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima, asilikali okonzekera nkhondo, amene zishango zawo zazikulu ndi mikondo yawo ing’onoing’ono zinkakhala zokonzeka.+ Nkhope zawo zinali ngati nkhope za mikango,+ ndipo liwiro lawo linali ngati la mbawala m’mapiri.+ 9 Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wachiwiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu, 10 wachinayi Misimana, wachisanu Yeremiya, 11 wa 6 Atai, wa 7 Elieli, 12 wa 8 Yohanani, wa 9 Elizabadi, 13 wa 10 Yeremiya, ndipo wa 11 anali Makibanai. 14 Amenewa anali a fuko la Gadi,+ atsogoleri a asilikali. Wamng’ono wa iwo akanatha kulimbana ndi asilikali 100, ndipo wamkulu wa iwo akanatha kulimbana ndi asilikali 1,000.+ 15 Awa ndi amene anawoloka mtsinje wa Yorodano+ m’mwezi woyamba* pamene mtsinjewo unasefukira mbali zake zonse.+ Kenako anathamangitsira kum’mawa ndi kumadzulo anthu onse amene anali kukhala m’zigwa.
16 Amuna ena a fuko la Benjamini ndi la Yuda anayenda mpaka kukafika kwa Davide, kumalo ovuta kufikako.+ 17 Pamenepo Davide anatuluka kukakumana nawo, ndipo anawauza kuti: “Ngati mwabwerera mtendere+ kwa ine kudzandithandiza, mtima wanga ugwirizana nanu.+ Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, pamene sindinalakwe ndi manja anga,+ Mulungu+ wa makolo athu aone zimenezo ndipo aweruze.”+ 18 Poyankha, Amasai mkulu wa asilikali 30 anagwidwa ndi mzimu,+ ndipo anati:
“Ifetu ndife anthu anu, inu a Davide, ndipotu tili kumbali yanu,+ inu mwana wa Jese.
Mtendere ukhale nanu, ndiponso mtendere ukhale ndi iye amene akukuthandizani,
Pakuti Mulungu wanu wakuthandizani.”+
Choncho Davide anawalandira ndi kuwaika pakati pa atsogoleri a asilikali.+
19 Analiponso ena a fuko la Manase amene anapanduka n’kupita kwa Davide pamene iye anabwera ndi Afilisiti+ kudzamenyana ndi Sauli. Koma Davide sanawathandize Afilisitiwo chifukwa olamulira awo ogwirizana+ atakambirana, anam’bweza chifukwa anati: “Ameneyu akhoza kukatitembenukira n’kugwirizana ndi mbuye wake Sauli, kenako akatidula mitu.”+ 20 Davide atapita ku Zikilaga,+ anthu ena a fuko la Manase anapita kumbali yake. Anthuwo anali Adinala, Yozabadi, Yediyaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu, ndi Ziletai. Aliyense wa amenewa anali mtsogoleri+ wa asilikali 1,000, a fuko la Manase. 21 Atsogoleriwa anathandiza Davide kulimbana ndi gulu la achifwamba,+ chifukwa atsogoleri onsewa anali amuna amphamvu+ ndi olimba mtima, ndipo anakhala atsogoleri a asilikali. 22 Tsiku ndi tsiku anthu anali kubwera+ kwa Davide kudzamuthandiza, mpaka anachuluka n’kukhala khamu lankhondo lalikulu,+ ngati khamu lankhondo la Mulungu.+
23 Tsopano nazi ziwerengero za atsogoleri a anthu okonzekera kumenya nkhondo amene anabwera kwa Davide ku Heburoni,+ kudzam’patsa ufumu+ wa Sauli malinga ndi lamulo la Yehova.+ 24 Anthu okonzekera kumenya nkhondo a fuko la Yuda, onyamula zishango zazikulu ndi mikondo ing’onoing’ono, analipo 6,800. 25 Anthu a fuko la Simiyoni, asilikali amphamvu ndi olimba mtima, analipo 7,100.
26 A fuko la Levi analipo 4,600. 27 Yehoyada ndiye anali mtsogoleri+ wa ana a Aroni,+ ndipo anali kuyang’anira anthu 3,700. 28 Panalinso Zadoki+ mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima ndi atsogoleri 22 a m’nyumba ya makolo ake.
29 A fuko la Benjamini,+ abale ake a Sauli,+ analipo 3,000. Kufikira pa nthawiyo, ambiri mwa anthu a fukolo, anali kulondera mosamala nyumba ya Sauli. 30 A fuko la Efuraimu analipo 20,800, amuna amphamvu+ ndi olimba mtima, otchuka m’nyumba ya makolo awo.
31 A hafu ya fuko la Manase,+ amene anatchulidwa mayina kuti adzalonge Davide ufumu, analipo 18,000. 32 A fuko la Isakara,+ amene anali ndi nzeru zotha kudziwa nthawi,+ ndi zimene Aisiraeli ayenera kuchita,+ analipo atsogoleri 200, ndipo iwo anali kulamulira abale awo onse. 33 A fuko la Zebuloni,+ onse oyenerera kupita kunkhondo, kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi zida zawo zonse zankhondo, analipo 50,000. Popita kwa Davide, iwo sanapite ndi mitima iwiri. 34 A fuko la Nafitali+ analipo atsogoleri 1,000. Pamodzi ndi iwowa panali onyamula zishango zazikulu ndi mikondo, okwanira 37,000. 35 A fuko la Dani, okafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo, analipo 28,600. 36 A fuko la Aseri,+ onse oyenerera kupita kunkhondo, kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo, analipo 40,000.
37 Kutsidya lina la Yorodano+ kunachokera a fuko la Rubeni, a fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase okhala ndi zida zonse zankhondo okwanira 120,000. 38 Onsewa anali amuna ankhondo, okhalira limodzi pamzere wa omenya nkhondo. Iwo anapita ndi mtima wathunthu+ ku Heburoni kukalonga Davide kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Ndiponso Aisiraeli ena onse otsala anali ndi mtima umodzi wolonga Davide ufumu.+ 39 Anthuwa anakhala kumeneko ndi Davide masiku atatu. Anali kudya ndi kumwa,+ chifukwa abale awo anali atawakonzekera. 40 Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara,+ Zebuloni,+ ndi Nafitali,+ anali kubweretsa chakudya pa abulu,+ ngamila, nyulu* ndi ng’ombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa.+ Anabweretsanso nkhuyu zouma zoumba pamodzi,+ mphesa zouma zoumba pamodzi,+ vinyo,+ mafuta,+ ng’ombe,+ ndi nkhosa.+ Anabweretsa zimenezi zambirimbiri, popeza mu Isiraeli munali chisangalalo+ chachikulu.
13 Tsopano Davide anakambirana ndi mkulu aliyense wa anthu 1,000, wa anthu 100 ndiponso mtsogoleri aliyense.+ 2 Iye anauza mpingo wonse wa Isiraeli kuti: “Ngati mukuona kuti ndi bwino ndiponso ngati zili zovomerezeka kwa Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kupita kwa abale athu ena m’madera onse a Isiraeli.+ Uthengawu upitenso kwa ansembe,+ ndi kwa Alevi,+ m’mizinda yawo+ yonse yokhala ndi malo odyetserako ziweto, kuti abwere kuno. 3 Kenako tikatenge likasa+ la Mulungu wathu n’kubwera nalo mpaka kwathu kuno.” Anatero chifukwa chakuti m’masiku a Sauli likasalo sanali kulisamala.+ 4 Choncho mpingo wonse unagwirizana nazo, chifukwa anthu onse anaona kuti ndi bwino kutero.+ 5 Chotero, Davide anasonkhanitsa+ Aisiraeli onse kuchokera kumtsinje wa Iguputo+ mpaka kukafika polowera ku Hamati,+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu.+
6 Atatero, Davide ndi Aisiraeli onse ananyamuka kupita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali m’dera la Yuda. Anapita kumeneko kukatenga likasa la Mulungu woona, Yehova, wokhala pa akerubi.+ Palikasa limeneli, amaitanirapo dzina lake. 7 Koma iwo ananyamulira likasa la Mulungu woonalo pangolo yatsopano+ kuchokera kunyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo+ anali kutsogolera ngoloyo. 8 Ndipo Davide ndi Aisiraeli onse anali kusangalala kwadzaoneni+ pamaso pa Mulungu woona. Anali kuimba nyimbo+ ndi azeze,+ zoimbira za zingwe,+ maseche,+ zinganga ndi malipenga.+ 9 Kenako anafika kumalo opunthira mbewu a Kidoni,+ ndipo Uza anatambasulira dzanja lake pa Likasa+ n’kuligwira, chifukwa ng’ombe zinatsala pang’ono kuligwetsa. 10 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, ndipo anamupha chifukwa anatambasula dzanja lake n’kugwira Likasa,+ moti Uza anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.+ 11 Zitatero, Davide anakwiya+ chifukwa mkwiyo wa Yehova unaphulikira Uza modzidzimutsa. Chotero malo amenewo amatchedwa dzina lakuti Perezi-uza* kufikira lero.
12 Tsiku limenelo, Davide anachita mantha kwambiri chifukwa cha Mulungu woona,+ ndipo anati: “Kodi ndibweretsa bwanji likasa la Mulungu woona kumene ine ndikukhala?”+ 13 Pamenepo Davide sanatenge Likasa kupita nalo kumene anali kukhala ku Mzinda wa Davide. M’malomwake, analipatutsira kunyumba ya Obedi-edomu+ Mgiti.+ 14 Likasa la Mulungu woona linakhalabe ndi banja la Obedi-edomu kunyumba kwake+ kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anapitiriza kudalitsa+ banja la Obedi-edomu, ndi zinthu zake zonse.
14 Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo+ anatumiza amithenga kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza,+ anthu omanga makoma, ndi anthu a ntchito zamatabwa kuti akamangire Davide nyumba.+ 2 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike+ mu Isiraeli, pakuti ufumu wake unakwezedwa kwambiri chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+
3 Davide anatenganso akazi ena+ mu Yerusalemu, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+ 4 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+ 5 Ibara,+ Elisua, Elipeleti,+ 6 Noga, Nefegi,+ Yafiya, 7 Elisama,+ Beliyada, ndi Elifeleti.+
8 Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli yense.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, anapita kukamenyana nawo. 9 Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kufunkha m’chigwa cha Arefai.+ 10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwaperekadi m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi m’manja mwako.” 11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero, Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” N’chifukwa chake malowo+ anawatcha Baala-perazimu. 12 Pa nthawiyi Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko.+ Ndiyeno Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+
13 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso ndi kuyamba kufunkha m’chigwacho.+ 14 Pamenepo Davide anafunsiranso+ kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Ayi usapite kukakumana nawo. Koma uwazembere ndipo ukawaukire kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 15 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka,+ ukatuluke n’kumenyana nawo+ chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola+ kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.” 16 Choncho Davide anachitadi monga mmene Mulungu woona anamulamulira,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibeoni+ mpaka kukafika ku Gezeri.+ 17 Chotero Davide anatchuka+ mpaka mbiri yake inamveka kumayiko onse. Ndipo Yehova anachititsa kuti mitundu yonse iziopa Davide.+
15 Davide anapitiriza kumanga nyumba+ zake mu Mzinda wa Davide, ndipo anakonza malo+ oikapo likasa la Mulungu woona, n’kulimangira hema. 2 Pa nthawi imeneyi m’pamene Davide ananena kuti: “Alevi okha ndiwo ayenera kunyamula likasa la Mulungu woona, chifukwa Yehova anasankha iwowa kuti azinyamula likasa la Yehova+ ndi kum’tumikira+ mpaka kalekale.”* 3 Ndiyeno Davide anasonkhanitsa Aisiraeli onse ku Yerusalemu+ kuti akanyamule likasa+ la Yehova, kupita nalo kumalo amene iye anakonza kuti akaliike.
4 Kenako Davide anaitanitsa ana a Aroni+ ndi Alevi. 5 Pa ana a Kohati panali Uriyeli+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 120. 6 Pa ana a Merari+ panali Asaya+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 220. 7 Pa ana a Gerisomu+ panali Yoweli+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 130. 8 Pa ana a Elizafana+ panali Semaya+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 200. 9 Pa ana a Heburoni panali Elieli mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 80. 10 Pa ana a Uziyeli+ panali Aminadabu mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 112. 11 Kuwonjezera pa amenewa, Davide anaitanitsa Zadoki+ ndi Abiyatara,+ omwe anali ansembe. Anaitanitsanso Alevi awa: Uriyeli,+ Asaya,+ Yoweli,+ Semaya,+ Elieli,+ ndi Aminadabu. 12 Tsopano Davide anawauza kuti: “Inuyo ndinu atsogoleri+ a nyumba ya makolo a Alevi. Choncho inu ndi abale anu mudziyeretse,+ ndipo mukatenge likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli n’kukaliika kumalo amene ine ndakonza kuti likakhaleko. 13 Chifukwa chakuti ulendo woyamba uja inuyo simunapite kukalitenga,+ mkwiyo wa Yehova Mulungu wathu unatiphulikira,+ pakuti sitinatsatire malangizo ake monga mwa mwambo wathu.”+ 14 Chotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ kuti akatenge likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli.
15 Ndiyeno ana a Alevi anakanyamula+ likasa la Mulungu woona, monga mmene Mose anawalamulira potsatira mawu a Yehova. Iwo analinyamula pamapewa awo pogwiritsa ntchito ndodo zake.+ 16 Tsopano Davide anauza atsogoleri a Alevi kuti aike m’malo awo abale awo oimba+ okhala ndi zipangizo zoimbira.+ Zipangizozo zinali zoimbira za zingwe,+ azeze,+ ndi zinganga.+ Anawauza kuti aimbe mokweza kuti nyimbo zachisangalalo zimveke.
17 Chotero Alevi anatenga Hemani+ mwana wa Yoweli n’kumuika pamalo ake. Kenako, pa abale ake, anatengapo Asafu+ mwana wa Berekiya n’kumuika pamalo ake. Pa abale awo, ana a Merari, anatengapo Etani+ mwana wa Kusaya n’kumuika pamalo ake. 18 Iwowa anawaika pamalo awo pamodzi ndi abale awo a gulu lachiwiri.+ Abale awowo anali Zekariya,+ Beni, Yaazieli, Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, ndiponso Obedi-edomu+ ndi Yeyeli, alonda a pachipata. 19 Panalinso oimba awa: Hemani,+ Asafu,+ ndi Etani, kuti aimbe zinganga zamkuwa mokweza.+ 20 Zekariya, Azieli,+ Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Maaseya, ndi Benaya, anali ndi zoimbira za zingwe zochunidwa kuti ziziimba Alamoti.*+ 21 Matitiya,+ Elifelehu, Mikineya, Obedi-edomu, Yeyeli, ndi Azaziya, anali ndi azeze+ ochunidwa kuti aziimba Seminiti,*+ kuti akhale otsogolera nyimbo. 22 Kenaniya+ ndiye anali mtsogoleri wa Alevi pa ntchito yonyamula katundu, ndipo anali kupereka malangizo onyamulira katundu, chifukwa anali katswiri pa ntchito imeneyi.+ 23 Berekiya ndi Elikana anali alonda+ a Likasa. 24 Sebaniya, Yosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya, ndi Eliezere, anali ansembe omwe anali kuimba malipenga mokweza+ patsogolo pa likasa la Mulungu woona. Obedi-edomu ndi Yehiya anali alonda a Likasa.
25 Koma Davide+ ndi akulu a Isiraeli+ ndiponso atsogoleri+a anthu 1,000 aliyense, anali kuyenda mosangalala+ kupita kunyumba kwa Obedi-edomu,+ kukatenga likasa la pangano la Yehova. 26 Mulungu woona atathandiza+ Alevi ponyamula likasa la pangano la Yehova, iwo anapereka nsembe ng’ombe zazing’ono zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.+ 27 Davide, Alevi onse onyamula Likasa, oimba, ndi Kenaniya+ mtsogoleri pa ntchito yonyamula katundu imene oimba+ anali kugwira, anavala malaya akunja odula manja, ansalu yabwino kwambiri. Koma Davide anavalanso efodi+ wansalu. 28 Aisiraeli onse anali kupita ndi likasa la pangano la Yehova akufuula mokondwera,+ ndiponso akuliza nyanga za nkhosa+ ndi malipenga.+ Iwo anali kuimbanso mokweza zinganga,+ zoimbira za zingwe, ndi azeze.+
29 Ndiyeno likasa la pangano+ la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi, ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kusangalala.+ Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.
16 Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+ 2 Davide atamaliza kupereka nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano,+ anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova.+ 3 Kuwonjezera apo, Aisiraeli onse, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi. 4 Ndiyeno Davide anaika Alevi+ ena kukhala otumikira+ pa likasa la Yehova kuti azikumbutsa+ anthu, kuyamika,+ ndi kutamanda+ Yehova Mulungu wa Isiraeli. 5 Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Panalinso Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu, ndi Yeyeli.+ Onsewa anali ndi zoimbira za zingwe ndi azeze,+ ndipo Asafu+ anali kuimba zinganga mokweza.+ 6 Benaya ndi Yahazieli, omwe anali ansembe, ankaimba malipenga+ nthawi zonse patsogolo pa likasa la pangano la Mulungu woona.
7 Pa tsiku limeneli m’pamene Davide anathandiza+ nawo kuyamika+ Yehova kudzera mwa Asafu+ ndi abale ake kwanthawi yoyamba, ndi nyimbo yakuti:
8 “Yamikani Yehova,+ anthu inu. Itanani pa dzina lake.+
Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake!+
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+
Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+
13 Inu mbadwa za Isiraeli mtumiki wake,+
Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+
14 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+ Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+
15 Kumbukirani pangano lake mpaka kalekale,+
Kumbukirani lonjezo limene anapereka, ku mibadwo 1,000,+
16 Kumbukirani pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+
Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki.+
17 Pangano limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,+
Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+
18 Pamene anati: ‘Ndidzakupatsa dziko la Kanani,+
Kuti likhale gawo la cholowa chako.’+
19 Pamene ananena zimenezi n’kuti inu muli ochepa,+
N’kuti muli ochepa kwambiri, komanso muli alendo m’dzikolo.+
20 Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+
Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+
21 Mulungu sanalole aliyense kuwachitira zachinyengo,+
Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
22 Iye anati: ‘Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,
Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+
23 Imbirani Yehova, inu nonse okhala padziko lapansi!+
Tsiku ndi tsiku lengezani chipulumutso chimene amapereka!+
24 Fotokozani za ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,
Ndiponso za ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25 Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+
Ndipo ndi woyenera kuopedwa kuposa milungu ina yonse.+
26 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake.+
Koma Yehova, ndiye anapanga kumwamba.+
28 Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,
M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+
29 M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake,+
Tengani mphatso n’kubwera nayo pamaso pake.+
Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+
30 Njenjemerani ndi mantha* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi!
Ndiponso dziko lapansi ndi lokhazikika,
Silidzagwedezeka ku nthawi zonse.+
31 Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale,+
Ndipo anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’+
32 Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,+
Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+
33 Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera chifukwa cha Yehova,+
Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+
34 Yamikani Yehova anthu inu, chifukwa iye ndi wabwino,+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
35 Nenani kuti: ‘Tipulumutseni, inu Mulungu wachipulumutso chathu,+
Tisonkhanitseni pamodzi ndi kutilanditsa kwa anthu a mitundu ina,+
Kuti titamande dzina lanu loyera,+ ndiponso kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+
36 Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli kuyambira kalekale mpaka kalekale.’”+
Ndiyeno anthu onse ananena kuti, “Ame!”* n’kutamanda Yehova.+
37 Kenako Davide anasiya Asafu+ ndi abale ake kumeneko pamaso pa likasa la Yehova, kuti azitumikira+ pamaso pa Likasalo nthawi zonse, malinga ndi zofunikira pa tsiku lililonse.+ 38 Anasiyanso Obedi-edomu ndi abale ake okwanira 68, ndiponso Obedi-edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa kukhala alonda a pachipata. 39 Anasiyanso Zadoki+ wansembe ndi abale ake ansembe kuchihema cha Yehova chimene chinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni,+ 40 kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova nthawi zonse paguwa lansembe zopsereza, m’mawa ndi madzulo, malinga ndi zonse zolembedwa m’chilamulo cha Yehova chimene analamula Aisiraeli.+ 41 Iwowa anali limodzi ndi Hemani+ ndi Yedutuni ndiponso amuna onse amene anasankhidwa+ mwa kutchulidwa mayina kuti aziyamika Yehova,+ chifukwa “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+ 42 Anasiya Hemani+ ndi Yedutuni+ limodzi ndi amuna aja kuti aziimba malipenga,+ zinganga ndi zipangizo zina zoimbira nyimbo ya Mulungu woona, ndipo ana+ a Yedutuni anali alonda a pachipata. 43 Pambuyo pake anthu onse ananyamuka, ndipo aliyense anapita kunyumba kwake.+ Nayenso Davide anapita kunyumba kwake n’kukadalitsa banja lake.
17 Ndiyeno Davide atangoyamba kukhala m’nyumba yake,+ anauza Natani+ mneneri kuti: “Ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza,+ koma likasa+ la pangano la Yehova likukhala m’chihema chansalu.”+ 2 Pamenepo Natani anauza Davide kuti: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu,+ chifukwa Mulungu woona ali nanu.”+
3 Tsopano usiku umenewo, Mulungu analankhula+ ndi Natani, kuti: 4 “Pita, ukauze Davide mtumiki wanga kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Si iwe amene udzandimangira nyumba yokhalamo.+ 5 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba, koma ndakhala m’hema ndi m’hema ndiponso m’chihema chopatulika+ ndi m’chihema chopatulika.+ 6 Pa nthawi yonse imene ndinali kuyendayenda+ pakati pa Isiraeli yense, kodi ndinalankhulapo n’kamodzi komwe kwa woweruza aliyense wa Isiraeli, amene ndinalamula kutsogolera anthu anga, mawu akuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu inu simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’+
7 “Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unali kusamalira nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli. 8 Ine ndidzakhala ndi iwe kulikonse kumene udzapite,+ ndipo ndidzawononga ndi kuchotsa adani ako onse+ pamaso pako. Ndidzakupangira dzina+ lofanana ndi dzina la anthu otchuka amene ali padziko lapansi.+ 9 Ndipo anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo ndi kuwakhazika pamalowo.+ Iwo adzakhaladi kumeneko ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu osalungama+ sadzawavutitsanso ngati mmene anachitira poyamba,+ 10 ngati mmene anachitira kuchokera masiku amene ndinaika oweruza+ kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli. Ndipo ndidzatsitsa adani ako onse.+ Tsopano ndikukuuza kuti: ‘Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakumangira nyumba.’*+
11 “‘“Masiku ako akadzakwana kuti ukakhale pamodzi ndi makolo ako,+ pamenepo ndithu ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako,+ imene idzakhala mmodzi wa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.+ 12 Iye ndiye adzandimangire nyumba,+ ndipo ndithu ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 13 Ine ndidzakhala atate wake+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Sindidzachotsa kukoma mtima kwanga kosatha pa iye+ monga mmene ndinachitira kwa amene analipo iwe usanakhalepo.+ 14 Ndidzamukhazikitsa iye kukhala woyang’anira nyumba yanga+ ndi ufumu wanga+ mpaka kalekale, ndipo mpando wake wachifumu+ sudzatha mpaka kalekale.”’”
15 Natani anauza Davide mawu onsewa ndi masomphenya onse amene anaona.+
16 Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova,+ ndipo inati: “Ndine yani ine,+ inu Yehova Mulungu? Ndipo nyumba yanga n’chiyani+ kuti mundifikitse pamene ndili pano?+ 17 Inu Mulungu,+ kuwonjezeranso pamenepa+ mwandiuza kuti nyumba ya ine mtumiki wanu idzakhazikika mpaka nthawi yam’tsogolo,+ ndipo inu Yehova Mulungu, mwanditenga ine ngati munthu woyenera kukwezedwa.+ 18 Ndiyeno ine Davide ndinganenenji kwa inu poona kuti mwandilemekeza ine mtumiki wanu,+ pamene inu mumandidziwa bwino ine mtumiki wanu?+ 19 Inu Yehova, chifukwa cha ine mtumiki wanu, komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,+ mwachita zazikulu zonsezi mwa kundidziwitsa zinthu zonse zazikulu zimene mudzachita.+ 20 Inu Yehova, palibe wofanana nanu,+ ndipo malinga ndi zonse zimene tamva ndi makutu athu, palibenso Mulungu wina koma inu nokha.+ 21 Ndi mtundu winanso uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu woona munawawombola monga anthu anu,+ ndi kudzipangira dzina mwa kuchita zinthu zazikulu+ ndi zochititsa mantha, popitikitsa mitundu+ pamaso pa anthu anu amene munawawombola ku Iguputo? 22 Inutu munapanga anthu anu Aisiraeli kuti akhaledi anthu anu+ mpaka kalekale. Ndipo inu Yehova munakhala Mulungu wawo.+ 23 Tsopano inu Yehova, mawu amene mwalankhula okhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake, akhale oona mpaka kalekale, ndipo chitani mmene mwanenera. 24 Dzina lanu+ likhale lokhulupirika ndi lokwezeka+ mpaka kalekale. Anthu anene kuti, ‘Yehova wa makamu+ Mulungu wa Isiraeli,+ ndiye Mulungu wa Isiraeli,’+ ndipo nyumba ya mtumiki wanu Davide ikhalitse pamaso panu.+ 25 Pakuti inu Mulungu wanga mwandiululira ine mtumiki wanu cholinga chanu chondimangira nyumba,+ n’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndapeza nthawi yopemphera pamaso panu. 26 Tsopano inu Yehova, ndinu Mulungu woona,+ ndipo mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+ 27 Choncho dalitsani nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Pakuti inu Yehova mwadalitsa nyumba ya mtumiki wanu, ndipo yadalitsika mpaka kalekale.”+
18 Pambuyo pake, Davide anapha Afilisiti+ ndi kuwagonjetsa, ndipo anawalanda mzinda wa Gati+ ndi midzi yake yozungulira. 2 Kenako anagonjetsa Mowabu,+ moti Amowabuwo anakhala atumiki a Davide ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+
3 Davide anapha Hadadezeri+ mfumu ya Zoba+ ku Hamati,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukakhazikitsa ulamuliro wake kumeneko. 4 Ndipo Davide analanda magaleta 1,000, anagwira amuna 7,000 okwera pamahatchi* ndi amuna 20,000 oyenda pansi.+ Kenako Davide anapundula*+ mahatchi onse a magaleta+ kusiyapo mahatchi a magaleta okwana 100. 5 Pamene Asiriya a ku Damasiko anabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba,+ Davide anapha amuna 22,000 a ku Siriya. 6 Ndiyeno Davide anamanga midzi ya asilikali m’dera la Asiriya a ku Damasiko,+ ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho kwa iye.+ Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+ 7 Davide anatenga zishango zozungulira+ zagolide zimene zinali ndi atumiki a Hadadezeri ndipo anabwera nazo ku Yerusalemu.+ 8 Komanso Davide anatenga mkuwa wambirimbiri ku Tibati+ ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezeri. Solomo anagwiritsa ntchito mkuwa umenewu kupangira thanki lamkuwa,+ zipilala+ ndi ziwiya zamkuwa.+
9 Tsopano Tou, mfumu ya Hamati,+ atamva kuti Davide wapha gulu lonse lankhondo la Hadadezeri+ mfumu ya Zoba, 10 nthawi yomweyo anatumiza mwana wake Hadoramu+ kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndi kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri ndi kumugonjetsa (pakuti Hadadezeri ndi Tou anali kumenyana kawirikawiri). Popita kwa Davide, Hadoramu anatenga zinthu zosiyanasiyana zagolide, zasiliva,+ ndi zamkuwa. 11 Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira+ Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide amene inalanda ku mitundu yonse,+ kuchokera ku Edomu, ku Mowabu,+ kwa ana a Amoni,+ Afilisiti,+ ndi Aamaleki.+
12 Nayenso Abisai+ mwana wa Zeruya,+ anapha Aedomu 18,000 m’chigwa cha Mchere.+ 13 Choncho anakhazikitsa midzi ya asilikali mu Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala akapolo a Davide.+ Yehova anali kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+ 14 Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli yense+ ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo kwa anthu ake onse.+ 15 Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa gulu lankhondo,+ ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 16 Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara anali ansembe, pamene Savisa+ anali mlembi. 17 Benaya+ mwana wa Yehoyada+ anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti,+ ndipo ana aamuna a Davide ndiwo anali ndi udindo waukulu kwambiri pamaso pa mfumu.+
19 Kenako, Nahasi+ mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndipo mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwa bambo akewo.+ 2 Zitachitika zimenezi, Davide anati: “Ndidzasonyeza Hanuni mwana wa Nahasi kukoma mtima kosatha,+ chifukwa bambo ake anandisonyeza kukoma mtima kosatha.”+ Chotero Davide anatumiza amithenga kuti akatonthoze Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo ake, ndipo atumiki a Davidewo anafika m’dziko la ana a Amoni+ kwa Hanuni kuti amutonthoze. 3 Koma akalonga a ana a Amoni anauza Hanuni kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani kuti alemekeze bambo anu pamaso panu? Kodi atumiki akewa sanabwere kwa inu kuti adzaonetsetse mzindawu ndi kuchita ukazitape,+ kuti adzaulande?”+ 4 Pamenepo Hanuni anatenga atumiki a Davide+ aja ndi kuwameta ndevu.+ Kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza m’matako,+ n’kuwauza kuti azipita.+ 5 Pambuyo pake anthu anauza Davide zimene zinachitikira atumiki ake aja, ndipo iye nthawi yomweyo anatumiza mthenga kuti akakumane nawo chifukwa atumikiwo anachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ kufikira ndevu zanu zitakula ndithu, kenako mudzabwere.”
6 Patapita nthawi, ana a Amoni anaona kuti akhala chinthu chonunkha+ kwa Davide. Choncho Hanuni+ ndi ana a Amoni anatumiza matalente* asiliva 1,000+ kuti akabwereke magaleta+ ndi kulemba ganyu asilikali okwera pamahatchi a ku Mesopotamiya, a ku Aramu-maaka+ ndi a ku Zoba.+ 7 Chotero anakabwereka magaleta 32,000,+ ndi kulemba ganyu mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake.+ Zitatero, iwowa anafika ndi kumanga misasa yawo pafupi ndi Medeba.+ Ndipo ana a Amoni anatuluka m’mizinda yawo ndi kusonkhana kuti akamenye nkhondo.
8 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza Yowabu+ ndi gulu lonse lankhondo pamodzi ndi amuna amphamvu.+ 9 Ndiyeno ana a Amoni anapita kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuchipata cha mzinda. Ndipo mafumu+ amene anabwera aja anali okhaokha kutchire.
10 Yowabu ataona kuti asilikali a adani ake akubwera mofulumira kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo kudzamenyana naye, nthawi yomweyo anatenga amuna ochita kusankhidwa mwapadera a mu Isiraeli ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti akumane ndi Asiriya.+ 11 Anthu ena onse anawapereka m’manja mwa Abisai+ m’bale wake, kuti afole mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi kukumana ndi ana a Amoni.+ 12 Ndiyeno anamuuza kuti: “Asiriya+ akandiposa mphamvu, iweyo undipulumutse.+ Koma ana a Amoni akakukulira mphamvu, ineyo ndifika kudzakupulumutsa.+ 13 Uchite zinthu mwamphamvu,+ ndipo tisonyeze kulimba mtima chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu.+ Yehova adzachita zimene zili zabwino m’maso mwake.”+
14 Choncho Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya,+ ndipo Asiriyawo anathawa+ pamaso pake. 15 Ana a Amoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa+ pamaso pa Abisai m’bale wake ndi kubwerera kumzinda.+ Kenako Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
16 Asiriya ataona kuti agonjetsedwa+ ndi Aisiraeli, anatumiza amithenga kukaitana Asiriya amene anali m’dera la ku Mtsinje,*+ pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa gulu lankhondo la Hadadezeri.
17 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse pamodzi ndi kuwoloka Yorodano kupita kukakumana nawo n’kukafola kuti amenyane nawo.+ Atafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Asiriya, Asiriyawo anayamba kumenyana naye. 18 Koma Asiriyawo anathawa+ pamaso pa Isiraeli, ndipo Davide anapha Asiriya 7,000 okwera magaleta, ndi asilikali 40,000 oyenda pansi. Komanso anapha Sofaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo.+ 19 Atumiki a Hadadezeri ataona kuti agonja pamaso pa Isiraeli,+ nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Davide n’kuyamba kumutumikira.+ Asiriya sanayesenso kupulumutsa ana a Amoni.+
20 Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Yowabu anatsogolera gulu lankhondo+ n’kukawononga dziko la ana a Amoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu. Tsopano Yowabu uja anapha anthu+ ku Raba n’kuwononga mzindawo. 2 Koma Davide anatenga chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,+ ndipo golide wa chisoticho anali wolemera talente* limodzi. Chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Kenako anthu anaveka Davide chisoticho. Zinthu zimene anafunkha mumzindawo zinali zochuluka kwambiri.+ 3 Anthu amene anali mumzindawo Davide anawatulutsa, ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito+ yocheka miyala, kusula zitsulo zakuthwa, ndiponso kusula nkhwangwa.+ Zimenezi n’zimene Davide anachitira mizinda yonse ya ana a Amoni. Pamapeto pake, Davide pamodzi ndi anthu onse anabwerera ku Yerusalemu.
4 Ndiyeno nkhondo imeneyi itatha, panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti+ ku Gezeri.+ Pa nthawi imeneyo Sibekai+ Mhusati anapha Sipa, amene anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai,+ moti Afilisiti anagonjetsedwa.
5 Kenako panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti, ndipo Elihanani+ mwana wa Yairi anapha Lami m’bale wake wa Goliyati+ Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu.+
6 Panabukanso nkhondo ina ku Gati,+ pa nthawi imene kunali munthu wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24 zonse pamodzi.+ Ameneyunso anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+ 7 Iye anali kutonza ndi kuderera+ Isiraeli, ndipo pamapeto pake Yonatani mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide, anamupha.
8 Anthu amenewa anali mbadwa za Arefai+ ku Gati.+ Iwo anaphedwa+ ndi dzanja la Davide ndi la atumiki ake.
21 Tsopano Satana anayamba kulimbana ndi Isiraeli polimbikitsa+ Davide kuti awerenge Aisiraeli. 2 Chotero Davide anauza Yowabu+ ndi atsogoleri a anthu kuti: “Pitani mukawerenge+ Aisiraeli kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo mubweretse chiwerengero chawo kwa ine kuti ndidziwe kuchuluka kwawo.”+ 3 Koma Yowabu anati: “Yehova awonjezere anthu ake kuwirikiza nthawi 100 pa chiwerengero chawo.+ Koma kodi mbuyanga mfumu, anthu onsewa si anu komanso si atumiki anu? Nanga n’chifukwa chiyani mbuyanga mukufuna kuchita zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mukufuna kupalamulitsa Isiraeli?”
4 Koma mawu a mfumu+ anaposa mawu a Yowabu moti Yowabu anachoka pamaso pa mfumu+ n’kuyenda mu Isiraeli yense. Kenako anabwerera ku Yerusalemu.+ 5 Atafika kumeneko, Yowabu anapereka chiwerengero chonse cha anthu kwa Davide. Aisiraeli onse analipo 1,100,000, amuna ogwira lupanga,+ ndipo amuna a Yuda ogwira lupanga analipo 470,000. 6 Koma Yowabu sanawerenge+ a fuko la Levi+ ndi la Benjamini, chifukwa anali ataipidwa ndi mawu a mfumu.
7 Zinthu zimenezi zinali zoipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo anapha Aisiraeli. 8 Davide ataona zimenezo, anauza Mulungu woona kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano, chonde, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu,+ pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+ 9 Pamenepo Yehova analankhula kwa Gadi,+ wamasomphenya wa Davide+ kuti: 10 “Pita, ukauze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndaika zilango zitatu pamaso pako.+ Sankha wekha chimodzi mwa zitatuzi chimene ukufuna kuti ndikuchitire.”’”+ 11 Choncho Gadi anapita kwa Davide+ ndi kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Sankhapo chimodzi: 12 Zaka zitatu za njala+ kapena miyezi itatu yoti adani anu akuseseni+ ndi kukuphani ndi lupanga lawo, kapenanso masiku atatu a lupanga la Yehova,+ lomwe ndi mliri+ umene udzagwe m’dziko lanu mpaka mngelo wa Yehova atasakaza+ madera onse a Isiraeli.’ Ndiye tandiuzani zoti ndikayankhe kwa Amene wanditumayo.” 13 Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, ndilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+
14 Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli, moti mu Isiraeli munafa anthu 70,000.+ 15 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu woona anatumiza mngelo ku Yerusalemu kuti akawononge mzindawo.+ Mngeloyo atangoyamba kuwononga, Yehova anaona zimenezo ndi kumva chisoni chifukwa cha tsokalo,+ choncho anauza mngelo amene anali kuwonongayo kuti: “Basi pakwanira!+ Tsitsa dzanja lako tsopano.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali ataimirira pafupi ndi malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi.+
16 Davide atakweza maso ake, anaona mngelo wa Yehova+ ataima m’malere, pakati padziko lapansi ndi kumwamba. Mngeloyo anali atagwira lupanga+ n’kuloza nalo Yerusalemu. Nthawi yomweyo, Davide ndi akulu amene anali naye, atavala ziguduli,*+ anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 17 Kenako Davide anauza Mulungu woona kuti: “Kodi si ine amene ndinalamula kuti awerenge anthu? Ndipo kodi si ine ndachimwa ndi kuchitadi cholakwa?+ Nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Chonde Yehova Mulungu wanga, dzanja lanu likhale pa ine ndi panyumba ya bambo anga, koma mliriwu usakhale pa anthu anu.”+
18 Ndiyeno mngelo wa Yehova anauza Gadi+ kuti auze Davide kuti Davideyo apite kumalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, n’kukamanga guwa lansembe la Yehova.+ 19 Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi amene anawanena m’dzina la Yehova.+ 20 Pamene zimenezi zinali kuchitika, Orinani+ anali akupuntha tirigu. Atatembenuka anaona mngelo, ndipo ana ake anayi amene anali naye limodzi anakabisala. 21 Davide uja anakafika kwa Orinani. Ndiye Orinani atakweza maso n’kuona Davide,+ nthawi yomweyo anachoka pamalo opunthira mbewu aja n’kukagwada pamaso pa Davide n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 22 Kenako Davide anauza Orinani kuti: “Ndipatse malo ako opunthira mbewuwa kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa. Ndikupatsa ndalama+ zake zonse.”+ 23 Koma Orinani anauza Davide kuti: “Ingotengani malowa akhale anu,+ ndipo mbuyanga mfumu chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Taonani, ineyo ndipereka ng’ombe+ kuti zikhale nsembe zopsereza ndi chopunthira tirigu+ kuti chikhale nkhuni,+ ndiponso ndipereka tirigu kuti akhale nsembe yambewu. Ndikupereka zonsezi.”+
24 Koma Mfumu Davide inauza Orinani kuti: “Iyayi, ineyo ndigula ndipo ndipereka ndalama zake zonse,+ chifukwa sindingatenge zinthu zako n’kupita nazo kwa Yehova kukapereka nsembe zopsereza popanda kulipira.” 25 Atatero, Davide anapatsa Orinani ndalama za malowo zolemera masekeli* 600 agolide.+ 26 Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza. 27 Kenako Yehova analankhula ndi mngelo uja,+ ndipo mngeloyo anabwezera lupanga lake m’chimake. 28 Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pamalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, anapitiriza kuperekera nsembe pamalopo.+ 29 Koma pa nthawiyo, chihema chopatulika cha Yehova chimene Mose anapanga m’chipululu ndi guwa lansembe zopsereza, zinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni.+ 30 Davide anali atasiya kupita kumeneko kukafunsira kwa Mulungu, chifukwa anali kuopa+ lupanga la mngelo wa Yehova.
22 Tsopano Davide anati: “Malo ano ndiwo nyumba+ ya Yehova Mulungu woona, ndipo guwa lansembe+ ili ndi la nsembe zopsereza za Isiraeli.”
2 Atatero, Davide analamula kuti asonkhanitse alendo+ okhala m’dziko la Isiraeli. Alendowo anawaika kukhala osema miyala,+ kuti azisema miyala yofanana mbali zonse,+ yomangira nyumba ya Mulungu woona. 3 Ndiyeno Davide anasonkhanitsa zitsulo zambirimbiri zopangira misomali ya zitseko za pazipata komanso zopangira zida zopanira zinthu. Anasonkhanitsanso mkuwa wambirimbiri wosatheka kuuyeza kulemera kwake.+ 4 Iye anasonkhanitsanso matabwa osawerengeka a mkungudza,+ popeza Asidoni+ ndi anthu a ku Turo+ anali atabweretsera Davide matabwa ambirimbiri a mkungudza. 5 Kenako Davide anati: “Mwana wanga Solomo ndi wamng’ono komanso wosakhwima,+ koma nyumba yoti adzamangire Yehova idzakhala yokongola,+ yaulemerero wosaneneka+ ndiponso yotchuka ndi yotamandika kumayiko onse. Ndiyetu ndim’konzere zipangizo zoti adzagwiritsire ntchito.” Chotero Davide asanafe, anasonkhanitsa zipangizo zambirimbiri pokonzekera ntchitoyo.+
6 Kuwonjezera pamenepo, anaitana mwana wake Solomo kuti amuuze za ntchito yomanga nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. 7 Ndipo Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Ineyo, ndinafunitsitsa ndi mtima wanga wonse+ kumanga nyumba ya dzina+ la Yehova Mulungu wanga. 8 Koma mawu a Yehova ananditsutsa, kuti: ‘Iweyo wakhetsa magazi ambirimbiri+ ndipo wamenya nkhondo zikuluzikulu.+ Sungamange nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wakhetsa magazi ambirimbiri pamaso panga padziko lapansi. 9 Taona, udzabala mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wabata, ndipo ndidzam’patsa mpumulo pakati pa adani ake onse omuzungulira.+ N’chifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo,*+ ndipo m’masiku ake ndidzakhazikitsa mtendere+ ndi bata pa Isiraeli. 10 Iyeyo ndi amene adzamanga nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana+ wanga, ndipo ine ndidzakhala atate wake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu+ pa Isiraeli ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’
11 “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendere bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulira za iwe.+ 12 Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso lamulo lotsogolera Isiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+ 13 Zinthu zidzakuyendera bwino+ ukayesetsa kutsatira malamulo+ ndi zigamulo+ zimene Yehova analamula+ Mose zokhudza Isiraeli. Khala wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+ Usaope+ kapena kuchita mantha.+ 14 Taona, pa nthawi ya masautso anga+ ndasonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwanira matalente* 100,000,+ ndi siliva wokwanira matalente 1,000,000. Koma n’zosatheka kuyeza kulemera kwa mkuwa+ ndi zitsulo+ chifukwa n’zochuluka kwambiri. Ndakonzanso matabwa ndi miyala, koma udzawonjezerapo zina. 15 Palinso antchito ambirimbiri, osema miyala,+ amisiri a miyala ndi a matabwa, ndiponso anthu onse odziwa ntchito zosiyanasiyana.+ 16 Golide, siliva, mkuwa, ndi zitsulo n’zosatheka kuziwerenga.+ Yamba kugwira ntchito imeneyi,+ ndipo Yehova akhale nawe.”+
17 Zitatha izi, Davide analamula akalonga onse a Isiraeli kuti athandize mwana wake Solomo. Iye anati: 18 “Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu?+ Kodi sanakupatseni mpumulo m’dziko lonseli?+ Pakuti iye wapereka m’manja mwanga anthu a m’dzikoli, ndipo dzikoli lagonjetsedwa pamaso pa Yehova+ ndi pa anthu ake. 19 Choncho funafunani Yehova Mulungu wanu+ ndi mtima wanu ndi moyo wanu.+ Yambani kumanga nyumba yopatulika+ ya Yehova Mulungu woona.+ Kenako mukatenge likasa+ la pangano la Yehova ndi ziwiya zopatulika za Mulungu woona n’kuziika m’nyumba ya dzina+ la Yehova imene imangidweyo.”
23 Davide anali atakalamba+ ndiponso atakhutira ndi masiku a moyo wake. Chotero analonga mwana wake Solomo+ kukhala mfumu ya Isiraeli. 2 Kenako anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli komanso ansembe+ ndi Alevi.+ 3 Atatero, Alevi anawerengedwa kuyambira azaka 30 kupita m’tsogolo.+ Anawerenga mwamuna aliyense wamphamvu, mmodzi ndi mmodzi,* ndipo onse anakwana 38,000. 4 Pakati pawo panali oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova okwana 24,000. Akapitawo+ ndi oweruza+ analipo 6,000. 5 Panalinso alonda 4,000 a pachipata+ ndi anthu 4,000 oimbira Yehova zitamando+ ndi zoimbira+ zimene Davide anati, “Zimenezi ndazipanga kuti tizitamandira Mulungu.”
6 Ndiyeno Davide anawagawa m’magulu+ ndi kuwapereka kwa ana a Levi.+ Anawapereka kwa Gerisoni, Kohati, ndi Merari. 7 M’banja la Gerisoni munali Ladani ndi Simeyi. 8 Ana a Ladani anali atatu. Panali Yehiela+ mtsogoleri wawo, Zetamu ndi Yoweli.+ 9 Ana a Simeyi anali atatu. Panali Selomoti, Hazieli ndi Harana. Amenewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo ya Ladani. 10 Ana a Simeyi anali Yahati, Zina,* Yeusi, ndi Beriya. Ana anayiwa anali a Simeyi. 11 Yahati anali mtsogoleri wawo, ndipo wachiwiri wake anali Ziza. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri aamuna, choncho anakhala nyumba imodzi ya makolo+ ndiponso gulu limodzi lokhala ndi udindo wofanana.
12 Ana a Kohati+ analipo anayi. Panali Amuramu, Izara,+ Heburoni+ ndi Uziyeli.+ 13 Ana aamuna a Amuramu anali Aroni+ ndi Mose.+ Koma Aroni anapatulidwa+ kuti iye ndi ana ake aziyeretsa Malo Oyera Koposa,+ mpaka kalekale. Komanso kuti azifukiza nsembe+ yautsi pamaso pa Yehova, kumutumikira,+ ndi kupereka madalitso+ m’dzina lake mpaka kalekale. 14 Ponena za Mose munthu wa Mulungu woona,+ ana ake anapitiriza kuwawerenga pamodzi ndi fuko la Levi.+ 15 Ana a Mose anali Gerisomu+ ndi Eliezere.+ 16 Ana a Gerisomu, mtsogoleri wawo anali Sebueli.+ 17 Ana a Eliezere, mtsogoleri wawo anali Rehabiya.+ Eliezere sanakhalenso ndi ana ena aamuna, koma Rehabiya anali ndi ana ochuluka kwambiri. 18 Ana a Izara,+ mtsogoleri wawo anali Selomiti.+ 19 Ana a Heburoni anali Yeriya amene anali mtsogoleri wawo, wachiwiri wake anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli, ndipo wachinayi anali Yekameamu.+ 20 Ana a Uziyeli+ anali Mika amene anali mtsogoleri wawo, ndipo Isiya anali wachiwiri wake.
21 Ana a Merari+ anali Mali ndi Musi.+ Ana a Mali anali Eleazara+ ndi Kisi. 22 Koma Eleazara anamwalira. Iye analibe ana aamuna koma aakazi. Choncho abale awo, ana a Kisi, anawatenga kukhala akazi awo.+ 23 Ana a Musi analipo atatu. Panali Mali, Ederi, ndi Yeremoti.+
24 Amenewa ndiwo anali ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo.+ Iwowa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo mmodzi ndi mmodzi anapatsidwa udindo potsata mndandanda wa mayina awo. Amenewa anali oti azigwira ntchito yotumikira+ panyumba ya Yehova kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo.+ 25 Davide anachita zimenezi popeza anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wapereka mpumulo kwa anthu ake,+ ndipo iye adzakhala mu Yerusalemu mpaka kalekale.+ 26 Ndipo Alevi sazinyamulanso chihema chopatulika kapena ziwiya zake zilizonse zogwiritsa ntchito potumikira kumeneko.”+ 27 Malinga ndi mawu omaliza+ a Davide, amenewa ndiwo ana a Levi amene anawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo. 28 Ntchito yawo inali yotumidwa ndi ana a Aroni+ pa utumiki wa panyumba ya Yehova m’mabwalo a nyumbayo,+ m’zipinda zodyeramo,+ pa ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika,+ ndiponso pa ntchito yotumikira panyumba ya Mulungu woona. 29 Anali kutumidwanso pa ntchito zokhudza mkate wosanjikiza,+ ufa wosalala+ wa nsembe yambewu, mikate yopyapyala+ yopanda chofufumitsa,+ makeke ophika m’chiwaya,+ ufa wokanya wosakaniza ndi mafuta,+ ndiponso miyezo yosiyanasiyana.+ 30 Analinso kutumikira m’mawa ulionse+ pa nthawi yoimirira+ kuti athokoze+ ndi kutamanda+ Yehova. Analinso kuchita zimenezi madzulo. 31 Anali kutumikiranso nthawi iliyonse yopereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo za chikondwerero.+ Nthawi zonse anali kutumikira popereka nsembezo kwa Yehova, malinga ndi ziwerengero zake, komanso potsata lamulo lake. 32 Ana a Leviwa analinso ndi ntchito yolondera+ chihema chokumanako, malo oyera,+ ndiponso yolondera abale awo, ana a Aroni, pa utumiki wa panyumba ya Yehova.+
24 Tsopano anagawa ana a Aroni m’magulu awo. Ana a Aroni anali Nadabu,+ Abihu,+ Eleazara,+ ndi Itamara.+ 2 Nadabu ndi Abihu+ anamwalira opanda ana aamuna bambo awo akali ndi moyo,+ koma Eleazara+ ndi Itamara anapitiriza kukhala ansembe. 3 Davide ndi Zadoki,+ yemwe anali wochokera mwa ana a Eleazara, ndiponso Ahimeleki,+ wochokera mwa ana a Itamara, anagawa ana a Aroniwo m’magulu a udindo pa utumiki wawo.+ 4 Koma ana a Eleazara anapezeka kuti anali ndi atsogoleri ambiri kuposa ana a Itamara. Choncho ana a Eleazara, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anawagawa m’magulu 16. Ndiponso ana a Itamara, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anawagawa m’magulu 8.
5 Pogawapo, anachita maere+ panyumba ya Eleazara pamodzi ndi panyumba ya Itamara. Anachita zimenezi chifukwa chakuti panafunika atsogoleri a pamalo oyera,+ ndi atsogoleri otumikira Mulungu woona, ochokera mwa ana a Eleazara ndiponso ochokera mwa ana a Itamara. 6 Kenako Semaya mwana wa Netaneli mlembi+ wa Alevi, anawalemba mayina pamaso pa mfumu, akalonga, wansembe Zadoki,+ Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara,+ ndiponso pamaso pa atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi.+ Anali kutenga nyumba imodzi ya makolo ya Eleazara+ ndi nyumba imodzi ya makolo ya Itamara.+
7 Atachita maere, zotsatira zake zinali motere: Woyamba anali Yehoyaribu,+ wachiwiri Yedaya, 8 wachitatu Harimu, wachinayi Seorimu, 9 wachisanu Malikiya, wa 6 Miyamini, 10 wa 7 Hakozi, wa 8 Abiya,+ 11 wa 9 Yesuwa, wa 10 Sekaniya, 12 wa 11 Eliyasibu, wa 12 Yakimu, 13 wa 13 Hupa, wa 14 Yesebeabu, 14 wa 15 Biliga, wa 16 Imeri, 15 wa 17 Heziri, wa 18 Hapizezi, 16 wa 19 Petahiya, wa 20 Yehezikeli, 17 wa 21 Yakini, wa 22 Gamuli, 18 wa 23 Delaya, ndipo wa 24 anali Maaziya.
19 Limeneli ndilo linali dongosolo+ la utumiki wawo,+ kuti azilowa m’nyumba ya Yehova malinga ndi mphamvu imene anapatsidwa+ kudzera m’dzanja la Aroni kholo lawo, monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli anamulamulira.
20 Ana a Levi amene anatsala anali motere: Pa ana a Amuramu+ panali Subaeli.+ Pa ana a Subaeli panali Yedeya. 21 Panalinso Rehabiya:+ Pa ana a Rehabiya panali Isiya mtsogoleri wawo. 22 Mwa mbadwa za Izara,+ panali Selomoti.+ Pa ana a Selomoti panali Yahati. 23 Ana a Heburoni+ anali Yeriya+ mtsogoleri wawo, Amariya wachiwiri, Yahazieli wachitatu, ndi Yekameamu wachinayi. 24 Pa ana a Uziyeli panali Mika. Pa ana a Mika+ panali Samiri. 25 M’bale wake wa Mika anali Isiya, ndipo pa ana a Isiya panali Zekariya.
26 Ana a Merari+ anali Mali+ ndi Musi.+ Pa ana a Yaaziya panali Beno. 27 Pa ana a Merari panali Yaaziya. Ana a Yaaziya anali Beno, Sohamu, Zakuri, ndi Ibiri. 28 Pa ana a Mali panali Eleazara amene analibe mwana.+ 29 Panalinso Kisi: Pa ana a Kisi panali Yerameeli. 30 Ana a Musi anali Mali,+ Ederi, ndi Yerimoti.+
Amenewa anali ana a Alevi potsata nyumba za makolo awo.+ 31 Iwonso anachita maere+ mofanana ndi mmene abale awo, ana a Aroni, anachitira pamaso pa Davide mfumu, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso pamaso pa atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi. Nyumba ya makolo+ ya wamkulu inali chimodzimodzi ndi nyumba ya makolo ya wamng’ono.
25 Ndipo Davide ndi atsogoleri+ a magulu a anthu otumikira,+ anapatula ena mwa ana a Asafu, a Hemani,+ ndi a Yedutuni,+ kuti azitumikira. Amuna atatuwa anali kulosera ndi azeze,+ zoimbira za zingwe,+ ndi zinganga.+ Mwa ana awo anatengamo amuna ena n’kuwaika pa udindo kuti azitumikira. 2 Pa ana a Asafu, anatengapo Zakuri, Yosefe,+ Netaniya, ndi Asarela.+ Ana ake amenewa anali kuyang’aniridwa ndi Asafuyo,+ amenenso anali mneneri wa mfumu. 3 Kwa Yedutuni,+ anatengako ana ake awa: Gedaliya,+ Zeri,+ Yesaiya,+ Simeyi, Hasabiya, ndi Matitiya,+ ana 6. Iwowa anali kuyang’aniridwa ndi Yedutuni bambo wawo, amene anali kulosera ndi zeze poyamika ndi potamanda Yehova.+ 4 Kwa Hemani,+ anatengako ana ake awa: Bukiya,+ Mataniya,+ Uziyeli,+ Sebueli, Yerimoti, Hananiya,+ Haneni, Eliyata,+ Gidaliti,+ Romamiti-ezeri,+ Yosebekasa,+ Maloti,+ Hotiri,+ ndi Mahazioti. 5 Onsewa anali ana a Hemani, wamasomphenya+ wa mfumu pa zinthu za Mulungu woona komanso wokweza nyanga* yake pofuna kutamanda Mulungu. Choncho Mulungu woona anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.+ 6 Ana onsewa anali kuyang’aniridwa ndi bambo awo poimba nyimbo m’nyumba ya Yehova. Ankaimba nyimbozo ndi zinganga,+ zoimbira za zingwe,+ ndi azeze,+ pochita utumiki wa panyumba ya Mulungu woona.
Koma Asafu, Yedutuni, ndi Hemani anali kuyang’aniridwa ndi mfumu.+
7 Chiwerengero chawo, pamodzi ndi abale awo ophunzitsidwa kuimbira Yehova,+ onse akatswiri,+ chinakwana 288. 8 Kenako anachita maere+ powagawira ntchito yoti azichita. Pochita maerewo, onse anali chimodzimodzi. Sanali kuyang’ana kuti uyu ndi wamng’ono kapena wamkulu,+ katswiri+ kapena wophunzira kumene.
9 Zotsatira za maerewo zinali motere: Maere oyamba anagwera Yosefe+ mwana wa Asafu, achiwiri anagwera Gedaliya+ (iye ndi abale ake ndi ana ake analipo 12), 10 achitatu anagwera Zakuri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 11 achinayi anagwera Iziri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 12 achisanu anagwera Netaniya,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 13 a 6 anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 14 a 7 anagwera Yesarela,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 15 a 8 anagwera Yesaiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 16 a 9 anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 17 a 10 anagwera Simeyi, ana ake ndi abale ake analipo 12, 18 a 11 anagwera Azareli,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 19 a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 20 a 13 anagwera Subaeli,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 21 a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 22 a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 23 a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake analipo 12, 24 a 17 anagwera Yosebekasa, ana ake ndi abale ake analipo 12, 25 a 18 anagwera Haneni, ana ake ndi abale ake analipo 12, 26 a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 27 a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake analipo 12, 28 a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake analipo 12, 29 a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake analipo 12, 30 a 23 anagwera Mahazioti,+ ana ake ndi abale ake analipo 12, 31 ndipo maere a 24 anagwera Romamiti-ezeri,+ ana ake ndi abale ake analipo 12.
26 Tsopano awa ndiwo magulu a alonda a pazipata:+ Pa mbadwa za Kora+ panali Meselemiya,+ mwana wa Kore wochokera mwa ana a Asafu. 2 Ndipo ana a Meselemiya anali awa: Woyamba anali Zekariya, wachiwiri Yediyaeli, wachitatu Zebadiya, wachinayi Yatiniyeli, 3 wachisanu Elamu, wa 6 Yehohanani, ndipo wa 7 anali Eliho-enai. 4 Obedi-edomu+ anali ndi ana awa: Woyamba anali Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinayi Sakari, wachisanu Netaneli, 5 wa 6 Amiyeli, wa 7 Isakara, ndipo wa 8 anali Peuletai, pakuti Mulungu anamudalitsa.+
6 Semaya mwana wa Obedi-edomu anabereka ana omwe anali olamulira nyumba ya bambo wawo, popeza anawo anali amuna odalirika ndi amphamvu. 7 Ana a Semaya anali Otini, Refaeli, Obedi, ndi Elizabadi. Elizabadi anali ndi abale ake odalirika, Elihu ndi Semakiya. 8 Onsewa anali mbadwa za Obedi-edomu. Iwowa, ana awo ndi abale awo anali odalirika ndi amphamvu potumikira. Onsewa, ochokera mwa Obedi-edomu, analipo 62. 9 Meselemiya+ anali ndi ana komanso abale ake, amuna odalirika okwanira 18. 10 Hosa, wochokera mwa ana a Merari anali ndi ana. Simuri anali mtsogoleri wa anawo ngakhale kuti sanali woyamba kubadwa,+ koma bambo akewo ndiwo anamusankha kukhala mtsogoleri.+ 11 Wachiwiri anali Hilikiya, wachitatu Tebaliya, ndipo wachinayi anali Zekariya. Ana onse a Hosa kuphatikizapo abale ake, analipo 13.
12 Pa magulu a alonda a pazipatawa, ntchito ya atsogoleri awo inali yofanana ndi ya abale awo,+ ndipo inali yotumikira panyumba ya Yehova. 13 Choncho anachita maere+ ofanana kwa wamng’ono ndi wamkulu potsata nyumba za makolo awo,+ kuti apeze ogwira ntchito pachipata chilichonse. 14 Maere a kum’mawa anagwera Selemiya.+ Anachitanso maere a Zekariya+ mwana wake, yemwe anali phungu+ wanzeru, ndipo maere ake anali oti akhale kumpoto.+ 15 Maere a Obedi-edomu anagwera kum’mwera, ndipo ana ake+ anaikidwa kuti azilondera nyumba zosungiramo zinthu.+ 16 Maere a Supimu ndi a Hosa+ anagwera kumadzulo pafupi ndi Chipata cha Saleketi, pamsewu wopita kumtunda. Gulu limodzi la alonda+ linakhala moyandikana ndi gulu lina la alonda.+ 17 Kum’mawa kunali Alevi 6, kumpoto anayi pa tsiku, kum’mwera anayi pa tsiku,+ ndipo kunyumba zosungiramo katundu+ awiriawiri. 18 Kukhonde la kumadzulo kumsewu, kunali anayi+ ndipo pakhonde panali awiri. 19 Amenewa anali magulu a alonda a pazipata a ana a mbadwa za Kora+ ndi mbadwa za Merari.+
20 Kumbali ya Alevi, Ahiya anali kuyang’anira chuma+ cha m’nyumba ya Mulungu woona, ndi chuma cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika.+ 21 Pa ana a Ladani,+ panali Yehieli.+ Ana amenewo anali mbadwa za Agerisoni kudzera mwa Ladani, ndipo anali atsogoleri a nyumba za makolo za Ladani Mgerisoni. 22 Ana a Yehieli anali Zetamu ndi Yoweli+ m’bale wake. Amenewa anali kuyang’anira chuma+ cha m’nyumba ya Yehova. 23 Panalinso mbadwa za Amuramu, za Izara, za Heburoni, ndi za Uziyeli,+ 24 ndipo Sebueli+ mwana wa Gerisomu mwana wa Mose, anali mtsogoleri panyumba zosungiramo katundu. 25 Abale ake obadwa mwa Eliezere,+ anali Rehabiya+ mwana wa Eliezere, Yesaiya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake, ndi Selomoti mwana wake. 26 Selomoti ameneyu pamodzi ndi abale ake anali kuyang’anira chuma chonse cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika. Amene anayeretsa zinthu zimenezi kukhala zopatulika+ anali Davide+ mfumu, atsogoleri a nyumba za makolo,+ atsogoleri a magulu a anthu 1,000, a magulu a anthu 100, ndi atsogoleri a asilikali. 27 Anayeretsa zinthu zimene anazitenga kunkhondo+ ndiponso zofunkha+ kuti azizigwiritsa ntchito panyumba ya Yehova. 28 Panalinso zinthu zonse zimene Samueli wamasomphenya,+ Sauli mwana wa Kisi, Abineri+ mwana wa Nera, ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ anaziyeretsa kukhala zopatulika. Chilichonse chimene munthu anachiyeretsa chinali kuyang’aniridwa ndi Selomiti ndi abale ake.
29 Kumbali ya mbadwa za Izara,+ panali Kenaniya ndi ana ake omwe anali akapitawo ndi oweruza+ Isiraeli, koma ntchito yawoyi sinali ya pakachisi.+
30 Kumbali ya Aheburoni,+ panali Hasabiya ndi abale ake, amuna odalirika+ okwanira 1,700. Iwowa anali ndi ntchito yoyang’anira Aisiraeli m’chigawo cha Yorodano kumadzulo, pa ntchito zonse za Yehova ndiponso pa ntchito zotumikira mfumu. 31 Kumbali ya Aheburoni kunalinso Yereya+ mtsogoleri wa Aheburoniwo malinga ndi mibadwo ya makolo awo. M’chaka cha 40+ cha ufumu wa Davide, iwo anafunafuna anthu ndipo anapeza amuna amphamvu ndi olimba mtima pakati pawo ku Yazeri+ ku Giliyadi.+ 32 Ndipo abale a Yereya, amuna odalirika+ komanso atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ analipo 2,700. Choncho mfumu Davide inawaika kuti aziyang’anira Arubeni, Agadi ndi hafu ya fuko la Manase+ pa nkhani iliyonse+ yokhudza Mulungu woona ndiponso yokhudza mfumu.
27 Tsopano nawa magulu a Aisiraeli amene anali m’gulu la asilikali a mfumu. M’magulu amenewa munali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ atsogoleri+ a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndi atsogoleri amene anali kusamalira magulu amenewa. Maguluwa anali kusinthanasinthana mwezi uliwonse pa chaka kutumikira+ mfumu, ndipo gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
2 Mtsogoleri wa gulu loyamba, la mwezi woyamba, anali Yasobeamu+ mwana wa Zabidiyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 3 Ana ena a Perezi+ anali akuluakulu a anthu amene anali kutumikira monga atsogoleri a asilikali. Nawonso ankatumikira mwezi woyamba. 4 Woyang’anira wa gulu la mwezi wachiwiri anali Dodai+ Muahohi,+ ndipo Mikiloti anali mtsogoleri wawo. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 5 Mtsogoleri wa gulu lachitatu, lotumikira mwezi wachitatu, anali Benaya+ mwana wa Yehoyada+ wansembe wamkulu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 6 Benaya+ ameneyu anali mwamuna wamphamvu pa amuna 30+ komanso anali mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Pagulu lakelo, mwana wake Amizabadi ndiye anali mtsogoleri. 7 Mtsogoleri wachinayi, wa mwezi wachinayi, anali Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo mwana wake Zebadiya anabwera pambuyo pake. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 8 Mtsogoleri wachisanu, wa mwezi wachisanu, anali Samuti+ Mwizirahiya. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 9 Mtsogoleri wa 6, wa mwezi wa 6, anali Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 10 Mtsogoleri wa 7, wa mwezi wa 7, anali Helezi+ Mpeloni,+ wochokera mwa ana a Efuraimu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 11 Mtsogoleri wa 8, wa mwezi wa 8, anali Sibekai+ Mhusati, wochokera mwa Azera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 12 Mtsogoleri wa 9, wa mwezi wa 9, anali Abi-ezeri+ Muanatoti,+ wochokera mwa Abenjamini. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 13 Mtsogoleri wa 10, wa mwezi wa 10, anali Maharai+ Mnetofa, wochokera mwa Azera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 14 Mtsogoleri wa 11, wa mwezi wa 11, anali Benaya+ Mpiratoni, wochokera mwa ana a Efuraimu.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 15 Mtsogoleri wa 12, wa mwezi wa 12, anali Heledai+ Mnetofa wa kubanja la Otiniyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.
16 Tsopano nawa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli:+ Mtsogoleri wa Arubeni anali Eliezere mwana wa Zikiri, wa Asimiyoni anali Sefatiya mwana wa Maaka, 17 wa Alevi anali Hasabiya mwana wa Kemueli, wa ana a Aroni anali Zadoki,+ 18 wa Ayuda anali Elihu+ mmodzi wa abale ake a Davide,+ wa Aisakara anali Omuri mwana wa Mikayeli, 19 wa Azebuloni anali Isimaya mwana wa Obadiya, wa Anafitali anali Yerimoti mwana wa Azirieli, 20 wa ana a Efuraimu anali Hoshiya mwana wa Azaziya, wa hafu ya fuko la Manase anali Yoweli mwana wa Pedaya, 21 wa hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi anali Ido mwana wa Zekariya, wa Abenjamini anali Yaasiyeli mwana wa Abineri,+ 22 ndipo mtsogoleri wa fuko la Dani anali Azareli mwana wa Yerohamu. Amenewa anali akalonga+ a mafuko a Isiraeli.
23 Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka 20 kutsika m’munsi, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisiraeli ngati nyenyezi zakumwamba.+ 24 Yowabu+ mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga anthu koma sanamalize.+ Kenako mkwiyo+ wa Mulungu unagwera Isiraeli chifukwa chowerenga anthuwo, ndipo chiwerengerocho sichinalembedwe pa zochitika za m’masiku a Mfumu Davide.
25 Azimaveti mwana wa Adieli anali kuyang’anira chuma cha mfumu.+ Yonatani mwana wa Uziya anali kuyang’anira chuma chosungidwa m’madera apafupi,+ m’mizinda,+ m’midzi ndi m’nyumba zosanja. 26 Eziri mwana wa Kelubu anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yolima minda.+ 27 Simeyi wa ku Rama anali woyang’anira minda ya mpesa,+ koma Zabidi wa ku Sifimi anali woyang’anira zinthu zonse zokhudza vinyo za m’minda ya mpesayo. 28 Baala-hanani Mgederi anali woyang’anira mitengo ya maolivi ndi ya mkuyu+ imene inali ku Sefela,+ ndipo Yowasi anali kuyang’anira mafuta.+ 29 Sitirai wa ku Sharoni+ anali kuyang’anira zoweta zimene anali kudyetsera ku Sharoni. Safati mwana wa Adilai anali kuyang’anira zoweta zimene zinali kuzigwa. 30 Obili Mwisimaeli+ anali kuyang’anira ngamila.+ Yedeya Mmeronoti anali kuyang’anira abulu aakazi. 31 Ndipo Yazizi Mhagara anali woyang’anira nkhosa. Anthu onsewa anali oyang’anira katundu wa Mfumu Davide.
32 Yonatani,+ mwana wa m’bale wake wa Davide, anali phungu wanzeru+ komanso mlembi. Yehiela mwana wa Hakimoni+ ndiye anali kuyang’anira ana a mfumu.+ 33 Ahitofeli+ anali phungu+ wa mfumu ndipo Husai+ Mwareki+ anali mnzake wa mfumu.+ 34 Kuwonjezera pa Ahitofeli panalinso Yehoyada mwana wa Benaya+ ndi Abiyatara,+ ndipo Yowabu+ anali mkulu wa asilikali a mfumu.
28 Davide anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli ku Yerusalemu. Akalongawo+ anali a mafuko ndi a magulu otumikira mfumu, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndiponso atsogoleri oyang’anira katundu yense+ ndi ziweto+ za mfumu ndi za ana ake.+ Panalinso nduna za panyumba ya mfumu+ ndi amuna amphamvu,+ ngakhale mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima. 2 Kenako Davide mfumu anaimirira ndipo anati:
“Ndimvereni inu abale anga ndi anthu anga. Ineyo ndinafunitsitsa mumtima mwanga+ kumanga nyumba yoti likasa la pangano la Yehova lizikhalamo, ndiponso yoti ikhale monga chopondapo mapazi+ cha Mulungu wathu, ndipo ndinakonzekera kuimanga.+ 3 Koma Mulungu woonayo anandiuza kuti; ‘Iwe sumanga nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wamenya nkhondo zambiri, ndiponso wakhetsa magazi ambiri.’+ 4 Komabe, m’nyumba yonse ya bambo anga+ Yehova Mulungu wa Isiraeli anasankha ineyo kuti ndikhale mfumu+ ya Isiraeli mpaka kalekale, popeza anasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri.+ M’nyumba ya Yuda anasankhamo nyumba ya bambo anga.+ Pa ana a bambo anga+ anavomereza ineyo+ kuti ndikhale mfumu ya Isiraeli yense. 5 Ndipo pa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana ambiri)+ anasankha mwana wanga Solomo+ kuti akhale pampando wachifumu+ wa ufumu wa Yehova, kuti alamulire Isiraeli.
6 “Kuwonjezera pamenepo, anandiuza kuti: ‘Mwana wako Solomo ndiye adzamanga nyumba yanga+ ndiponso mabwalo anga, chifukwa ndam’sankha kuti akhale mwana wanga+ ndipo ine ndidzakhala atate wake.+ 7 Akamatsatira malamulo anga+ ndi zigamulo zanga+ ndi mtima wonse ngati mmene akuchitira lero, ine ndidzakhazikitsa ufumu wake+ ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’ 8 Tsopano mwaima pamaso pa Aisiraeli onse, amene ndi mpingo wa Yehova,+ ndiponso Mulungu wathu akumva zimenezi.+ Choncho samalani ndi kutsatira malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti dziko labwinoli+ likhale lanu ndi kuti mudzasiyire ana anu obwera pambuyo panu monga cholowa chawo mpaka kalekale.
9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+ 10 Tsopano taona, Yehova wakusankha kuti umange nyumba yopatulika yoti azikhalamo. Limba mtima ndipo gwira ntchitoyi.”+
11 Atatero, Davide anapatsa Solomo mwana wake mapulani akamangidwe+ ka khonde+ ndi nyumba zake, zipinda zake zosungiramo katundu,+ zipinda zake zakudenga,*+ zipinda zake zamkati zosalowa kuwala kwambiri, ndi nyumba yokhalamo chivundikiro chophimba machimo.+ 12 Panalinso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu+ zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyeramo+ kuzungulira kachisi, chuma cha nyumba ya Mulungu woona, ndi chuma cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika.+ 13 Anam’patsanso malangizo okhudza magulu+ a ansembe ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wa panyumba ya Yehova, ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wa panyumba ya Yehova. 14 Anayezeratu golide, golide wa ziwiya zonse+ za ntchito zosiyanasiyana, ndi siliva wa ziwiya zonse zasiliva za ntchito zosiyanasiyana. 15 Anayezanso kulemera kwa zoikapo nyale+ zagolide ndi nyale zake zagolide, malinga ndi kulemera kwa zoikapo nyale zosiyanasiyana ndi nyale zake, komanso kulemera kwa zoikapo nyale zasiliva malinga ndi kulemera kwa choikapo nyale ndi nyale zake mogwirizana ndi ntchito zosiyanasiyana za zoikapo nyalezo. 16 Anayeza golide malinga ndi kulemera kwa matebulo osiyanasiyana oikapo mkate wosanjikiza,+ ndipo anayezanso siliva wa matebulo asiliva. 17 Anayezanso mafoloko, mbale zolowa,+ mitsuko, zinthu zonse zagolide woyenga bwino ndi mbale zing’onozing’ono zagolide zolowa,+ malinga ndi kulemera kwa mbale zing’onozing’ono zosiyanasiyana zolowa, komanso mbale zing’onozing’ono zasiliva zolowa, malinga ndi kulemera kwa mbale zing’onozing’ono zosiyanasiyana zolowa. 18 Anayezanso golide woyengedwa bwino wa guwa lansembe la zofukiza+ malinga ndi kulemera kwake, ndiponso golide wa chifaniziro cha galeta,+ kutanthauza akerubi+ agolide otambasula mapiko awo kuphimba likasa la pangano la Yehova. 19 “Zonsezi zalembedwa+ chifukwa chakuti dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo anandithandiza kumvetsa mbali zake zonse za mapulani a kamangidwe kake.”+
20 Kenako Davide anauza Solomo mwana wake kuti: “Limba mtima,+ ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope+ kapena kuchita mantha+ chifukwa Yehova Mulungu, Mulungu wanga, ali ndi iwe.+ Sadzakutaya+ kapena kukusiya, kufikira ntchito yonse yokhudza utumiki wa nyumba ya Yehova itatha. 21 Tsopano ndikukupatsa magulu a ansembe+ ndi a Alevi+ ogwira ntchito zonse za panyumba ya Mulungu woona. Pa ntchito yonseyi, uli ndi amisiri odzipereka+ odziwa ntchito zosiyanasiyana,+ ndi akalonga,+ ndiponso anthu onse. Onsewa ndi okonzeka kuchita monga mwa mawu ako.”
29 Tsopano mfumu Davide inauza mpingo wonse+ kuti: “Solomo mwana wanga, amene Mulungu wamusankha,+ ndi wamng’ono+ ndi wosakhwima. Koma ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa chinyumba chachikuluchi, si cha munthu ayi,+ koma ndi cha Yehova Mulungu. 2 Ine ndakonzekera nyumba ya Mulungu wanga ndi mphamvu zanga zonse.+ Ndakonzekera+ golide+ wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa, zitsulo+ zopangira zinthu zachitsulo, ndi matabwa+ opangira zinthu zamatabwa. Ndakonzekeranso miyala ya onekisi,+ miyala yomanga ndi simenti yolimba, miyala yokongoletsera, miyala yamitundumitundu yamtengo wapatali, ndi miyala yambirimbiri ya alabasitala. 3 Chifukwa chakuti ndikusangalala+ ndi nyumba ya Mulungu wanga, ndili ndi chuma chapadera+ chomwe ndi golide ndi siliva. Ndikupereka chuma chimenechi kunyumba ya Mulungu wanga kuwonjezera pa zonse zimene ndakonzera nyumba yopatulikayo.+ 4 Chumacho chili motere: Matalente* 3,000 a golide wa ku Ofiri,+ matalente 7,000 a siliva woyengedwa bwino wokutira makoma a nyumbazo, 5 golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, ndi siliva woti amisiri adzagwirire ntchito zonse. Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?”+
6 Pamenepo, akalonga+ a nyumba za makolo,+ akalonga+ a mafuko a Aisiraeli, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ ndi a magulu a anthu 100,+ ndiponso atsogoleri oyang’anira ntchito+ za mfumu, anayamba kupereka zinthu mwa kufuna kwawo. 7 Chotero iwo anapereka golide wokwanira matalente 5,000, madariki* 10,000, siliva wokwanira matalente 10,000, mkuwa wokwanira matalente 18,000, ndi zitsulo zokwanira matalente 100,000.+ Anapereka zonsezi kuti zigwire ntchito panyumba ya Mulungu woona. 8 Miyala iliyonse yamtengo wapatali imene munthu aliyense anali nayo, anaipereka ku chuma cha panyumba ya Yehova, chomwe Yehiela+ Mgerisoni+ anali kuyang’anira. 9 Anthuwo anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.+ Nayonso mfumu Davide inasangalala kwambiri.+
10 Kenako Davide anatamanda+ Yehova pamaso pa mpingo wonse,+ kuti: “Mudalitsike+ inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ atate wathu, kuyambira kalekale mpaka kalekale. 11 Inu Yehova, ukulu,+ mphamvu,+ kukongola,+ ulemerero,+ ndi ulemu+ ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu.+ Ufumu+ ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse.+ 12 Chuma+ ndi ulemerero+ zimachokera kwa inu. Inu mumalamulira+ chilichonse. M’dzanja lanu muli mphamvu+ ndi nyonga,+ ndipo dzanja lanu limatha kukweza+ ndiponso kupereka mphamvu kwa onse.+ 13 Tsopano inu Mulungu wathu, tikukuyamikani+ ndi kutamanda+ dzina lanu lokongola.+
14 “Ndine ndani ine,+ ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi?+ Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu,+ ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu. 15 Ifetu ndife alendo pamaso panu, komanso okhala m’dziko la eni+ monga analili makolo athu onse. Masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi,+ ndipo ndife osakhalitsa. 16 Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zochuluka zonsezi zimene takonzekera kuti tikumangireni nyumba, nyumba ya dzina lanu loyera, zachokera m’dzanja lanu ndipo zonse ndi zanu.+ 17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu. 18 Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli makolo athu,+ thandizani anthu awa kuti apitirizebe kukhala ndi mtima wodzipereka woterewu,+ ndiponso kuti akutumikireni ndi mtima wawo wonse.+ 19 Mupatse Solomo mwana wanga mtima wathunthu+ kuti asunge malamulo anu,+ maumboni* anu,+ ndi kuti achite zonse. Ndiponso kuti amange chinyumba chachikulu+ chimene ndakonzeratu zipangizo zake.”+
20 Kenako Davide anauza mpingo wonse kuti:+ “Tsopano tamandani+ Yehova Mulungu wanu!” Choncho mpingo wonse unayamba kutamanda Yehova Mulungu wa makolo awo, ndipo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ kwa Yehova ndi kwa mfumu. 21 Anthuwo anayamba kupereka nsembe+ kwa Yehova, ndipo anali kupereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova mpaka tsiku lotsatira. Anapereka ng’ombe zamphongo zazing’ono 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ana a nkhosa amphongo 1,000, ndi nsembe zake zachakumwa.+ Iwo anapereka nsembe zambirimbiri za Isiraeli yense.+ 22 Pa tsiku limenelo, iwo anadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Yehova.+ Kachiwirinso, analonga Solomo mwana wa Davide kukhala mfumu,+ ndi kum’dzoza pamaso pa Yehova kukhala mtsogoleri.+ Anadzozanso Zadoki+ kukhala wansembe. 23 Chotero, Solomo anayamba kukhala pampando wachifumu wa Yehova+ monga mfumu m’malo mwa Davide bambo wake, ndipo ankalamulira bwino.+ Aisiraeli onse anali kumumvera. 24 Akalonga onse+ ndi amuna amphamvu,+ ndiponso ana onse a Mfumu Davide,+ anali kugonjera Solomo mfumu. 25 Yehova anapitiriza kukweza Solomo+ pamaso pa Aisiraeli onse, ndi kum’patsa ulemu waukulu wachifumu kuposa mfumu ina iliyonse imene inalamulira Isiraeli iye asanakhale mfumu.+
26 Kunena za Davide mwana wa Jese, iye analamulira Isiraeli yense.+ 27 Masiku onse amene iye analamulira Isiraeli anakwana zaka 40.+ Ku Heburoni analamulira zaka 7,+ ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+ 28 Pamapeto pake, iye anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali,+ wokhutira ndi masiku, chuma+ ndi ulemerero.+ Kenako Solomo mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 29 Nkhani zokhudza Davide mfumu, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa pakati pa mawu a Samueli wamasomphenya,*+ Natani+ mneneri, ndiponso pakati pa mawu a Gadi+ wamasomphenya. 30 Nkhanizo zinalembedwa pamodzi ndi nkhani zonse zokhudza ufumu wake, zochita zake zamphamvu, ndi zinthu+ zimene zinachitika kwa iye, kwa Isiraeli, ndi kwa maufumu onse a m’mayiko osiyanasiyana.+
Dzina lakuti “Pelegi” limatanthauza, “Kugawika” ndiponso “Mtsinje.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “ana.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Dzina lakuti “Akari” limatanthauza “Mavuto, Wovutitsa.” Pa Yoswa 7:1, 18, akutchedwa “Akani.”
Dzina limeneli likuchokera ku mawu amene m’Chiheberi amatanthauza “ululu.”
Dzinali limatanthauza, “Chigwa cha Amisiri.”
Kutanthauza, Yerobowamu Wachiwiri.
Mawu ake enieni, “mizinda.”
M’Malemba achiheberi mulibe dzina lake.
Kutanthauza, “Ndi Tsoka.”
N’kutheka kuti “Refa” ndi “Resefe” anali ana a Beriya.
Kapena kuti “Yoswa.”
Pavesi 34 akutchedwa Semeri.
Mawu ake enieni, “nyumba ya chihema.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati, “kugwaza.”
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda, kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Dzinali limatanthauza, “Mkwiyo Woyakira Uza.”
Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Alamoti,” ndi mawu achiheberi a chuni. Mawuwa sadziwika tanthauzo lake, koma mwina ankatanthauza mawu a sapulano a atsikana, kapena mawu okwera kwambiri a anyamata.
“Seminiti,” ndi mawu achiheberi a chuni cha nyimbo, mwina otanthauza mawu oimbidwa motsitsa kapena kuti mwabesi.
Kapena kuti, “imvani kupweteka kwambiri.”
Mawuwa amatanthauza kuti, “zikhale momwemo.”
Mawu akuti “nyumba” akutanthauza mzera wa mafumu.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Anali kuwapundula mwa kudula mtsempha wa kuseri kwa mwendo wam’mbuyo.
Onani Zakumapeto 12.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani Zakumapeto 12.
Ena amati “masaka.”
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Dzinali limatanthauza, “Wamtendere.”
Onani Zakumapeto 12.
Mawu ake enieni, “mutu ndi mutu.”
Ameneyu ndi Ziza wotchulidwa m’vesi 11.
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Kapena kuti, “zakutsindwi.”
Onani Zakumapeto 12.
“Dariki” ndi ndalama yagolide yachiperisiya. Onani Zakumapeto 12.
Kapena kuti “zikumbutso.”
Zikuoneka kuti wamasomphenya anali munthu amene Mulungu ankamuchititsa kuti azitha kudziwa chifuniro cha Mulunguyo.