Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 2 Kings 1:1-25:30
  • 2 Mafumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Mafumu
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Mafumu

Mafumu Wachiwiri

kapena, malinga ndi Baibulo lachigiriki la Septuagint, MAFUMU WACHINAYI

1 Ahabu+ atamwalira, Amowabu+ anayamba kupandukira+ Isiraeli.

2 Kenako Ahaziya ali m’nyumba yake ku Samariya, anagwa+ kuchokera pachipinda chapadenga+ kudzera pachibowo chotchinga, ndipo anavulala. Atatero anatuma amithenga kuti: “Pitani kwa Baala-zebubu+ mulungu wa ku Ekironi,+ mukafunse+ ngati ndichire matenda angawa.”+ 3 Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anauza Eliya wa ku Tisibe+ kuti: “Nyamuka ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu+ kuti mupite kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi? 4 Tsopano Yehova wanena kuti: “Pabedi wakwerapo sutsikapo, chifukwa umwalira ndithu.”’”+ Eliya atalankhula mawu amenewa, anachoka.

5 Amithenga aja atabwerera kwa Ahaziya, nthawi yomweyo iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mwabwerera?” 6 Amithengawo anamuyankha kuti: “Munthu winawake anabwera kudzakumana nafe ndipo watiuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene yakutumani ndipo mukaiuze kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu kuti utumize anthu kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi? Pa chifukwa chimenechi, pabedi wakwerapo sutsikapo, chifukwa umwalira ndithu.’”’”+ 7 Pamenepo mfumuyo inawafunsa kuti: “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo n’kukuuzani zimenezi anali kuoneka bwanji?” 8 Iwo anayankha kuti: “Munthuyo anavala chovala chaubweya+ ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake.”+ Mfumuyo itangomva zimenezi, inanena kuti: “Ndi Eliya wa ku Tisibe.”

9 Ndiyeno mfumuyo inatumiza kwa Eliya mtsogoleri wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Mtsogoleriyo atafika, anam’peza atakhala pamwamba pa phiri ndipo anamuuza kuti: “Munthu wa Mulungu woona+ iwe, mfumu yanena kuti, ‘Tsika!’” 10 Koma Eliya anayankha mtsogoleri wa asilikali 50 uja kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu, moto+ utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Ndipo moto unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50.+

11 Kenako mfumuyo inam’tumiziranso mtsogoleri wina wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Mtsogoleriyo anauza Eliya kuti: “Munthu wa Mulungu woona iwe, mfumu yanena kuti, ‘Tsika msanga!’”+ 12 Koma Eliya anawayankha kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu woona, moto utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Ndipo moto wa Mulungu unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50.

13 Mfumuyo inatumizanso mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Koma mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 ameneyo anabwera n’kugwada+ pamaso pa Eliya ndipo anayamba kumuchonderera+ kuti awachitire chifundo. Iye anati: “Inu munthu wa Mulungu woona, chonde moyo wanga+ ndi moyo wa atumiki anu 50 awa ukhale wamtengo wapatali+ m’maso mwanu. 14 Pajatu moto unatsika kumwamba n’kunyeketsa+ atsogoleri awiri aja ndi magulu awo a asilikali 50, koma tsopano moyo wanga ukhale wamtengo wapatali m’maso mwanu.”

15 Pamenepo mngelo wa Yehova anauza Eliya kuti: “Tsika upite naye limodzi, usamuope.”+ Choncho Eliya ananyamuka n’kupita pamodzi ndi mtsogoleri uja kwa mfumu. 16 Atafika, Eliya anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti watumiza anthu+ kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi+ ngati kuti ku Isiraeli kulibe Mulungu amene ungafunsireko mawu ake, sutsika pabedi wakwerapo, chifukwa umwalira ndithu.’” 17 Patapita nthawi, Ahaziya anamwalira,+ mogwirizana ndi mawu+ a Yehova amene Eliya ananena. Kenako Yehoramu*+ anayamba kulamulira m’malo mwake chifukwa Ahaziya analibe mwana wamwamuna. Iye anayamba kulamulira m’chaka chachiwiri cha Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda.

18 Zinthu zina zimene Ahaziya+ anachita zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

2 Yehova atatsala pang’ono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+ 2 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu,+ sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapita ku Beteli.+ 3 Ndiyeno ana a aneneri+ amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo.+ Khalani chete.”

4 Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Khala apa Elisa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko. 5 Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo. Khalani chete.”+

6 Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yorodano.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo. 7 Ndiyeno panali ana a aneneri 50 omwe anakaima chapatali poonekera.+ Koma Eliya ndi Elisa anakaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. 8 Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika uku ndi uku, chotero iwo anawoloka pouma.+

9 Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.”+ Elisa anati: “Chonde, magawo awiri+ a mzimu+ wanu abwere kwa ine.”+ 10 Eliya anati: “Wapempha+ chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.”

11 Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta*+ lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba.+ 12 Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo, ndipo anali kufuula kuti: “Bambo anga, bambo anga!+ Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Zitatero, Elisa sanamuonenso Eliya. Kenako Elisa anagwira zovala zake n’kuzing’amba pakati.+ 13 Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi, ndipo anabwerera kukaima m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano. 14 Ali pamenepo, anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija n’kumenya nacho madzi a mtsinjewo,+ n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?”+ Atamenya madziwo, pang’onopang’ono madziwo anagawanika uku ndi uku, ndipo Elisa anawoloka.

15 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu+ wa Eliya uli pa Elisa.” Chotero anapita kukakumana naye n’kugwada+ pamaso pake mpaka nkhope zawo pansi. 16 Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu, bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu+ wa Yehova wamunyamula ndipo wam’ponya paphiri linalake kapena m’chigwa.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatumize.” 17 Koma iwo anam’kakamiza mpaka iye anachita manyazi, choncho anati: “Atumizeni.” Chotero anatumiza amuna 50 kukafunafuna Eliya. Iwo anam’funafuna kwa masiku atatu koma sanam’peze. 18 Ndiyeno anabwerera kwa Elisa ku Yeriko.+ Anthuwo atafika, Elisa ananena kuti: “Kodi ine sindinakuuzeni kuti, ‘Musapite’?”

19 Patapita nthawi, anthu a mumzindawo anauza Elisa kuti: “Mzindawu uli pamalo abwino+ monga mmene inu mbuyathu mukuonera, koma madzi+ ake ndi oipa, ndipo nthaka ikuchititsa akazi kupita padera.”+ 20 Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni mbale yaing’ono yatsopano yolowa, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anam’bweretseradi mbaleyo. 21 Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo n’kuponyapo mchere uja,+ n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino.+ Sadzachititsanso imfa kapena kuchititsa akazi kupita padera.’” 22 Madziwo ndi abwino kufikira lero+ mogwirizana ndi mawu amene Elisa ananena.

23 Kenako Elisa ananyamuka kupita ku Beteli.+ Akuyenda kukwezeka chitunda, anyamata ena+ amene anachokera mumzinda anayamba kumunyoza mokuwa+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe!+ Choka kuno wadazi iwe!” 24 Pomalizira pake Elisa anatembenuka ndipo anawaona. Atatero anawaitanira tsoka+ m’dzina la Yehova. Kenako zimbalangondo ziwiri zazikazi+ zinatuluka m’thengo n’kukhadzulapo anyamata 42.+ 25 Elisa anapitiriza ulendo wake mpaka kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera n’kupita ku Samariya.

3 Yehoramu+ mwana wa Ahabu, anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya m’chaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya Yuda, ndipo analamulira kwa zaka 12. 2 Iye anali kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ koma osati ngati mmene anachitira bambo ake+ kapenanso mmene anachitira mayi ake. Iye anachotsa chipilala chopatulika+ cha Baala chimene bambo ake anapanga.+ 3 Komabe, anaumirira osasiya kuchita machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa+ nawo Isiraeli.

4 Mesa+ mfumu ya Mowabu anali woweta nkhosa. Ankapereka kwa mfumu ya Isiraeli ana a nkhosa 100,000, ndi nkhosa zamphongo zosameta ubweya zokwana 100,000 monga msonkho. 5 Ahabu atangomwalira,+ mfumu ya Mowabu inapandukira+ mfumu ya Isiraeli. 6 Pa nthawiyo, Mfumu Yehoramu inatuluka ku Samariya n’kukasonkhanitsa+ Aisiraeli onse. 7 Kuwonjezera apo, inatumiza uthenga kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, wakuti: “Mfumu ya Mowabu yandipandukira. Kodi upita nane kukamenya nkhondo ku Mowabu?” Yehosafati anayankha kuti: “Inde ndipita.+ Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu ako ndi anthu anga ndi amodzi.+ Mahatchi anga n’chimodzimodzi ndi mahatchi ako.” 8 Yehosafati anafunsa kuti: “Tidzera njira iti?” Yehoramu anayankha kuti: “Tidzera njira ya m’chipululu cha Edomu.”+

9 Choncho mfumu ya Isiraeli, mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu+ ananyamuka n’kuyenda mozungulira kwa masiku 7. Koma kuchipululuko kunalibe madzi oti anthuwo amwe pamodzi ndi ziweto zimene anali kuyenda nazo. 10 Kenako mfumu ya Isiraeli inati: “Kalanga ine! Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu!”+ 11 Pamenepo Yehosafati anati:+ “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova?+ Ngati alipo tiyeni tifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye.”+ Ndiyeno mmodzi mwa atumiki a mfumu ya Isiraeli anayankha kuti: “Kuli Elisa+ mwana wa Safati, amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.”+ 12 Atamva zimenezo, Yehosafati anati: “Mawu a Yehova ali mwa iye.” Choncho mfumu ya Isiraeli, Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anapita kwa Elisa.

13 Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Ndili nanu chiyani?+ Pitani kwa aneneri+ a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.” Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu.”+ 14 Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova wa makamu Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira,+ pakanakhala kuti palibe Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikanakuyang’anani+ n’komwe kapena kukusamalani.+ 15 Anthu inu, ndiitanireni woimba zeze.”+ Woimba zezeyo atangoyamba kuimba, dzanja+ la Yehova linakhala pa Elisa. 16 Kenako iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Mukumbekumbe ngalande m’chigwa* chonsechi,+ 17 chifukwa Yehova wanena kuti: “Anthu inu simuona mphepo kapena mvula, koma chigwa chonsechi chidzaza madzi.+ Inu pamodzi ndi ziweto zanu, ndithu mumwa madziwo.”’+ 18 Zimenezi ndi zinthu zazing’ono kwambiri pamaso pa Yehova,+ ndipo ndithu apereka Amowabu m’manja mwanu.+ 19 Choncho mukagwetse mzinda uliwonse wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,+ mzinda uliwonse wabwino kwambiri,+ ndi mtengo uliwonse wabwino.+ Mukatseke akasupe onse amadzi, ndipo mukawononge malo alionse abwino mwa kuponyapo miyala.”

20 Ndiyeno zinachitika n’zakuti, pa nthawi yopereka nsembe yambewu+ m’mawa,+ anangoona madzi akuyenda kuchokera cha ku Edomu, ndipo malo onsewo anadzaza madzi.

21 Amowabu onse atamva kuti kwabwera mafumu kudzamenyana nawo, anasonkhanitsa amuna ambiri kuyambira amsinkhu wopita ku nkhondo+ kupita m’tsogolo, ndipo anakaima m’malire. 22 Atadzuka m’mawa, dzuwa linawalira pamadzi aja, moti kwa Amowabu amene anali kutsidya linalo, madziwo anaoneka ofiira ngati magazi. 23 Ataona zimenezi, anayamba kunena kuti: “Amenewa ndi magazi. Ndithu mafumu aja aphedwa ndi lupanga. Ndiye kuti aphana okhaokha. Tsopano Amowabu inu, tiyeni tikafunkhe!”+ 24 Iwo atalowa mumsasa wa Aisiraeli,+ nthawi yomweyo Aisiraeli ananyamuka n’kuyamba kuwapha. Amowabuwo anayamba kuthawa,+ ndipo Aisiraeli anathamangitsa Amowabuwo n’kumawapha mpaka kukalowa ku Mowabu. 25 Ndiyeno Aisiraeliwo anayamba kugwetsa mizinda.+ Pamalo alionse abwino, aliyense anali kuponyapo mwala mpaka kudzaza malo onsewo. Anatseka kasupe aliyense wamadzi+ ndi kugwetsa mtengo uliwonse wabwino.+ Koma miyala ya mzinda wa Kiri-hareseti+ yokha anaisiya. Oponya miyala anazungulira mzindawo n’kuuponya miyala.

26 Mfumu ya Mowabu itaona kuti nkhondo yaikulira, nthawi yomweyo inatenga amuna 700 amalupanga pofuna kudutsa kuti ikapeze mfumu ya Edomu,+ koma iwo analephera. 27 Pomalizira pake, mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu m’malo mwake, n’kumupereka+ nsembe yopsereza pakhoma. Choncho panabuka mkwiyo waukulu kwambiri wokwiyira Aisiraeli, motero iwo analeka kumenyana ndi mfumu ya Mowabu ndipo anabwerera kwawo.

4 Mayi wina yemwe anali mmodzi wa akazi a ana+ a aneneri, anafika kwa Elisa n’kulankhula mokweza kuti: “Mtumiki wanu yemwe anali mwamuna wanga anamwalira. Inu mukudziwa bwino kuti mtumiki wanuyo anali woopa+ Yehova. Tsopano kwabwera wangongole+ kudzatenga ana anga onse awiri kuti akakhale akapolo ake.” 2 Ndiyeno Elisa anamuyankha kuti: “Ndiye ndikuchitire chiyani?+ Tanena, uli ndi chiyani m’nyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti: “Ine kapolo wanu ndilibe chilichonse m’nyumba mwanga, ndili ndi kamtsuko ka mafuta kokha basi.”+ 3 Elisa anati: “Pita ukabwereke zotengera zopanda kanthu kwa anthu amene ukukhala nawo pafupi. Usakabwereke zochepa ayi. 4 Ukakatero, iwe ndi ana akowo mukalowe m’nyumba ndipo mukatseke chitseko. Ndiyeno uzikathira mafutawo m’zotengerazo. Zimene zadzaza uzikaziika pambali.” 5 Atamuuza zimenezi, mayiyo ananyamuka.

Iye ndi ana ake atakadzitsekera m’nyumba, anawo an’kamuikira zotengera zija pafupi, iye n’kumathiramo mafuta.+ 6 Zotengera zija zitadzaza, mayiyo anauza mwana wake kuti: “Bweretsa chotengera china.”+ Koma mwanayo anayankha kuti: “Palibenso chotengera china.” Pamenepo mafuta aja analeka.+ 7 Kenako anapita kwa munthu wa Mulungu woona uja kukamuuza zomwe zinachitikazo. Munthu wa Mulungu woonayo anati: “Pita ukagulitse mafutawo ndi kubweza ngongole zako,+ ndipo ndalama zotsalazo zithandize iwe ndi ana ako.”+

8 Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu.+ Kumeneko kunali mayi wina wodziwika. Mayiyo anaumiriza+ Elisa kuti adye chakudya. Nthawi zonse Elisa akamadutsa, anali kupatukira kumeneko kukadya chakudya. 9 Patapita nthawi, mayiyo anauza mwamuna wake+ kuti: “Tsopano ndikudziwa kuti munthu amene amadzera kuno nthawi zonse uja, ndi munthu woyera wa Mulungu.+ 10 Tiyeni tim’mangire kachipinda kapadenga*+ kukhoma.* M’kachipindamo timuikire bedi, tebulo, mpando, ndi choikapo nyale,+ kuti akabwera azikhala mmenemo.”+

11 Monga mwa nthawi zonse, tsiku lina Elisa anabwera, ndipo analowa m’kachipinda kapadengako n’kugona mmenemo. 12 Ndiyeno Elisa anauza mtumiki wake Gehazi+ kuti: “Itana mayi wachisunemu+ uja.” Choncho iye anamuitana kuti adzaime pamaso pa Elisa. 13 Ndiyeno Elisa anauza Gehazi kuti: “Muuze kuti, ‘Mwavutika ndi kutisamalira,+ kodi tingakuchitireni chiyani?+ Kodi pali chinachake choti tikakunenereni kwa mfumu,+ kapena kwa mkulu+ wa asilikali?’” Koma mayiyo anayankha kuti: “Ayi, ndilibe vuto lililonse, chifukwa ndikukhala mwamtendere pakati pa anthu a mtundu wanga.”+ 14 Elisa anati: “Ndiye timuchitire chiyani?” Gehazi anayankha kuti: “Mayiyutu alibe mwana wamwamuna,+ ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.” 15 Nthawi yomweyo Elisa anati: “Muitane.” Choncho Gehazi anamuitana ndipo mayiyo anaima pakhomo. 16 Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala mukuyangata mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Iyayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.”

17 Komabe, monga mmene Elisa ananenera, mayiyo anatenga pakati n’kubereka mwana wamwamuna+ nthawi ngati yomwe ija chaka chotsatira.+ 18 Mwanayo akukula, tsiku lina anapita kwa bambo ake kumunda pamodzi ndi antchito okolola, monga mwa nthawi zonse.+ 19 Kumeneko mwanayo analira kwa bambo ake kuti: “Mutu wanga ine! Mayo ine mutu wanga!”+ Kenako bambo akewo anauza wantchito wawo kuti: “M’nyamule mwanayu upite naye kwa mayi ake.”+ 20 Wantchitoyo ananyamuladi mwanayo n’kupita naye kwa mayi ake. Mayi akewo anamukhazika pamwendo mpaka masana, kenako mwanayo anamwalira.+ 21 Ndiyeno mayiyo ananyamula mwanayo n’kukamugoneka pabedi+ la munthu wa Mulungu woona+ uja. Atatero anatuluka n’kutseka chitseko. 22 Kenako anaitana mwamuna wake ndipo anamuuza kuti: “Nditumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi wamkazi. Ndikufuna ndithamangire kwa munthu wa Mulungu woona uja.”+ 23 Mwamuna wakeyo anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukufuna kupitako lero? Lero si tsiku lokhala mwezi+ kapena pasabata.” Koma mayiyo anayankha kuti: “Palibe kanthu.” 24 Ndiyeno mayiyo anakwera bulu wake wamkazi+ n’kuuza wantchito wake kuti: “Kwera bulu utsogole. Uzithamanga, usayende pang’onopang’ono chifukwa cha ine, pokhapokha ndikakuuza.”

25 Chotero mayiyo anayenda n’kukafika kwa munthu wa Mulungu woona uja paphiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu woonayo ataona mayiyo chapatali, anauza mtumiki wake Gehazi kuti:+ “Taona, mayi wachisunemu uja uyo! 26 Thamanga ukakumane naye. Ukamufunse kuti: ‘Kodi muli bwino? Mwamuna wanu ali bwanji? Nanga mwana wanu ali bwanji?’” Mayiyo anayankha kuti: “Onse ali bwino.” 27 Mayiyo atafika kwa munthu wa Mulungu woona paphiripo, nthawi yomweyo anam’gwira mapazi.+ Gehazi ataona zimenezo, anabwera pafupi kuti am’kankhe mayiyo.+ Koma munthu wa Mulungu woonayo+ anamuuza kuti: “Musiye,+ mtima wake ukum’pweteka kwambiri.+ Koma Yehova wandibisira,+ sanandiuze.” 28 Kenako mayiyo anati: “Kodi ndinakupemphani mwana mbuyanga? Kodi ine sindinanene kuti, ‘Musandipatse chiyembekezo chabodza’?”+

29 Nthawi yomweyo Elisa anauza Gehazi+ kuti: “Kokera chovala chako m’chiuno ndipo uchimange.+ Tenga ndodo yangayi+ uzipita. Ukakumana ndi munthu aliyense panjira usamupatse moni,+ ndipo munthu akakupatsa moni, usamuyankhe. Ukaike ndodo yangayi pankhope ya mwanayo.”+ 30 Pamenepo mayi wa mwanayo anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu+ sindikusiyani.”+ Choncho Elisa ananyamuka n’kupita pamodzi ndi mayiyo. 31 Gehazi anatsogola ndipo anaika ndodo ija pankhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena chizindikiro chosonyeza kuti ali moyo.+ Chotero iye anabwerera kukakumana ndi Elisa n’kumuuza kuti: “Mwana uja sanauke.”+

32 Kenako Elisa analowa m’nyumbamo ndipo anapeza mwana wakufayo atam’goneka pabedi lake lija.+ 33 Ndiyeno Elisa analowa m’chipindamo n’kutseka chitseko. M’chipindamo analimo awiriwiri.+ Atatero anayamba kupemphera kwa Yehova.+ 34 Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada n’kuweramira mwanayo.+ Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, manja ake anawaika pa manja a mwanayo. Anakhalabe chowerama choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kufunda. 35 Anayambanso kuyenda uku ndi uku m’nyumbamo. Atatero anapitanso kukaweramira mwanayo. Pamenepo mwanayo anayamba kuyetsemula mpaka maulendo 7, kenako anapenya.+ 36 Ndiyeno Elisa anaitana Gehazi n’kumuuza kuti: “Itana mayi wachisunemu uja.”+ Gehazi anaitana mayiyo ndipo anabweradi kwa Elisa. Elisayo anauza mayiyo kuti: “Nyamulani mwana wanu.”+ 37 Pamenepo mayiyo anapita kwa Elisa n’kugwada pamapazi ake, n’kumuweramira mpaka pansi.+ Kenako ananyamula mwana wakeyo ndipo anatuluka naye.+

38 Pambuyo pake, Elisa anabwerera ku Giligala,+ ndipo m’dzikolo munali njala.+ Tsopano ana+ a aneneri anakhala pamaso pake.+ Patapita nthawi, iye anauza mtumiki wake kuti:+ “Teleka mphika waukulu kuti uwaphikire chakudya ana a aneneriwa.”+ 39 Choncho wina anapita kutchire kukathyola masamba,+ ndipo anapezako kamtengo koyanga, n’kuthyolapo mphonda zakutchire kudzaza pachovala chake. Atatero anabwera nazo n’kuziduladula. Kenako anazithira mumphika uja, koma iwo sankazidziwa bwinobwino. 40 Pambuyo pake anazikhuthula n’kupatsa ana a aneneriwo kuti adye. Atangoyamba kudya chakudyacho, analankhula mokweza kuti: “Inu munthu wa Mulungu woona,+ muli poizoni mumphikamu!”+ Ndipo sanathenso kudya. 41 Ndiyeno Elisa anati: “Bweretsani ufa.” Atathira ufawo mumphikamo, ananena kuti: “Apatseni anthuwa kuti adye.” Atatero, mumphikamo munalibenso chakupha chilichonse.+

42 Ndiyeno kunabwera munthu wina kuchokera ku Baala-salisa.+ Iye anabweretsera+ munthu wa Mulungu woonayo mkate wa zipatso zoyambirira kucha,+ mitanda 20 ya mkate wa balere,+ ndi tirigu* watsopano m’thumba lake. Choncho Elisa anati: “Gawira anthuwa kuti adye.”+ 43 Koma woperekera chakudyayo anati: “Ndingagawire bwanji chakudya chimenechi anthu 100?”+ Elisa ananena kuti: “Gawira anthuwa kuti adye, pakuti Yehova wanena kuti, ‘Anthuwa adya mokwanira chakudyachi, ndipo chitsala.’”+ 44 Munthuyo atamva zimenezi, anagawira anthuwo chakudyacho. Iwo anadya mpaka chakudyacho chinatsala, mogwirizana ndi mawu a Yehova.+

5 Tsopano munthu winawake dzina lake Namani,+ mkulu wa gulu la asilikali a mfumu ya Siriya, anakhala munthu wofunika pamaso pa mbuye wake. Iye anali wolemekezeka, chifukwa Yehova anapulumutsa Siriya+ kudzera mwa iyeyo. Munthuyo anasonyeza kuti anali wamphamvu ndi wolimba mtima, ngakhale kuti anali wakhate. 2 Tsopano magulu achifwamba a Asiriya+ anapita kudziko la Isiraeli komwe anakagwirako kamtsikana n’kupita nako kwawo.+ Kenako kamtsikanako kanayamba kutumikira mkazi wa Namani. 3 Patapita nthawi, kamtsikanako kanauza+ mbuye wake wamkazi kuti: “Mbuyanga akanapita kwa mneneri+ amene ali ku Samariya, akanam’chiritsa khate lake.”+ 4 Pambuyo pake mbuye wake anauzidwa zimene kamtsikana ka ku Isiraeli kaja kananena.+

5 Ndiyeno mfumu ya Siriya inauza Namani kuti: “Nyamuka, ndikupatsa kalata upite kwa mfumu ya Isiraeli.” Choncho iye ananyamuka atatenga+ matalente* 10 a siliva, masekeli 6,000 a golide,+ ndi zovala 10.+ 6 Kenako Namani anabweretsa kalatayo+ kwa mfumu ya Isiraeli. Kalatayo inati: “Pa nthawi imene mukulandira kalatayi, ndatumiza kwa inu mtumiki wanga Namani, kuti mum’chiritse khate lake.” 7 Mfumu ya Isiraeli itawerenga kalatayo, nthawi yomweyo inang’amba+ zovala zake n’kunena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu,+ wotha kupha munthu kapena kum’siya wamoyo?+ Munthu uyu wanditumizira wodwala kuti ndim’chiritse khate lake. Taonani amuna inu kuti munthuyu akufuna kukangana nane.”+

8 Elisa munthu wa Mulungu woona atangomva kuti mfumu ya Isiraeli yang’amba zovala zake,+ anatumiza uthenga kwa mfumuyo, wakuti: “N’chifukwa chiyani mwang’amba zovala zanu? Muuzeni abwere kwa ine kuti adziwe kuti ku Isiraeli kuli mneneri.”+ 9 Chotero Namani anabwera ndi mahatchi ake ndi magaleta ake ankhondo ndipo anaima pakhomo pa nyumba ya Elisa. 10 Koma Elisa anatuma mthenga kukamuuza kuti: “Pita ukasambe+ maulendo 7+ mumtsinje wa Yorodano, kuti mnofu wako ubwerere mwakale ndi kuti iweyo+ ukhale woyera.” 11 Namani atamva zimenezi anapsa mtima+ n’kunyamuka kuti azipita, ndipo anati: “Ine ndinati,+ ‘Abwera kudzaima pafupi ndi ine n’kuitana dzina la Yehova Mulungu wake. Kenako ayendetsa dzanja lake uku ndi uku pamwamba pa malo amatendawo n’kundichiritsa khate langali.’ 12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko+ si yabwino kuposa madzi+ onse a mu Isiraeli? Kodi sindingasambe mmenemo n’kuyeretsedwa?”+ Atatero anatembenuka n’kumapita, ali wokwiya kwambiri.+

13 Tsopano atumiki ake anamutsatira ndipo anamufunsa kuti: “Bambo wanga,+ kodi mneneriyo akanakuuzani kuti muchite chinthu chachikulu, simukanachita? Nanga bwanji poti wangokuuzani kuti, ‘Kasambeni ndi kuyeretsedwa’?” 14 Namani atamva zimenezi, anatsetserekera ku Yorodano n’kukamira maulendo 7, mogwirizana ndi mawu a munthu wa Mulungu woona+ uja. Pambuyo pake, mnofu wake unabwerera mwakale moti unakhala ngati mnofu wa kamnyamata,+ ndipo anakhala woyera.+

15 Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.” 16 Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira,+ sindilandira.”+ Ndiyeno Namani anayamba kum’kakamiza kuti alandire, koma iye anakanabe. 17 Pamapeto pake, Namani anati: “Ngati mukukana, chonde ine mtumiki wanu, mundipatseko dothi+ lotha kunyamulidwa ndi nyulu* ziwiri, chifukwa sindidzaperekanso nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse kwa milungu ina, koma kwa Yehova basi.+ 18 Pa nkhani yotsatirayi, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu: Ndikakalowa m’kachisi wa Rimoni+ pamodzi ndi mbuyanga, nditam’chirikiza+ mbuyangayo pomugwira dzanja pamene akugwadira+ Rimoni, ine n’kugwada nawo m’kachisi wa Rimoni, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani imeneyi.”+ 19 Elisa atamva zimenezi anamuuza kuti: “Pita mu mtendere.”+ Choncho iye anachoka ndipo anayenda kaulendo ndithu.

20 Kenako Gehazi,+ amene anali kutumikira Elisa, munthu wa Mulungu woona+ uja, ananena mumtima mwake kuti: “Mbuyanga wangomusiya Namani+ Msiriya uja osalandira zimene anabweretsa. Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndim’thamangira kuti ndikatengeko zinthu zina kwa iye.”+ 21 Ndiyeno Gehazi anathamangira Namani. Namani ataona kuti munthu akum’thamangira, nthawi yomweyo anatsika pagaleta lake kuti akumane naye. Kenako anati: “N’kwabwino?”+ 22 Gehazi anayankha kuti: “Inde n’kwabwino. Mbuyanga+ wandituma+ kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri,+ kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+ 23 Pamenepo Namani anamuuza kuti: “Chabwino. Tenga matalente awiri.” Anamuumiriza+ mpaka anam’mangira matalente awiri a siliva m’matumba awiri, ndi zovala ziwiri. Anapereka zinthuzo kwa atumiki ake awiri kuti am’nyamulire.

24 Atafika ku Ofeli, nthawi yomweyo Gehazi anawalandira katunduyo ndipo anamuika m’nyumba.+ Kenako anauza amunawo kuti azipita, ndipo iwo anapitadi. 25 Ndiyeno Gehazi anapita kukaima pafupi ndi mbuyake.+ Kenako Elisa anam’funsa kuti: “Kodi unapita kuti, Gehazi?” Iye anayankha kuti: “Ine mtumiki wanu sindinapite kulikonse.”+ 26 Pamenepo Elisa anati: “Kodi mtima wanga sunali nawe limodzi pamene munthuyo anali kutembenuka ndi kutsika pagaleta lake kuti akumane nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira siliva, zovala, minda ya maolivi, minda ya mpesa, nkhosa, ng’ombe, antchito aamuna, kapena antchito aakazi?+ 27 Tsopano khate+ la Namani limamatira iweyo ndi mbadwa zako mpaka kalekale.”*+ Nthawi yomweyo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa, atachita khate loyera kuti mbuu.+

6 Tsopano ana+ a aneneri anauza Elisa kuti: “Taonani, malo+ amene tikukhala pamaso panu pano tikupanikizanapo.+ 2 Tiyeni tipite ku Yorodano, kuti aliyense akatengeko mtengo woti tikamangire+ malo okhala.” Choncho Elisa anati: “Pitani.” 3 Ndiyeno wina anati: “Tiyeni mupitire limodzi ndi atumiki anu.” Elisa atamva anati: “Chabwino, ndipita nawo.” 4 Choncho iye anapita nawo limodzi. Atafika ku Yorodano iwo anayamba kudula mitengo.+ 5 Munthu wina akudula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka+ n’kugwera m’madzi. Pamenepo munthuyo anayamba kulira kuti: “Kalanga ine mbuyanga!+ Nkhwangwayo inali yobwereka!”+ 6 Munthu wa Mulungu woonayo anafunsa kuti: “Yagwera pati?” Iye anamusonyeza pamene inagwera. Nthawi yomweyo Elisa anadula kamtengo n’kukaponya pamalopo ndipo nkhwangwayo inayandama.+ 7 Ndiyeno anamuuza kuti: “Itenge.” Munthuyo anatambasula dzanja lake msangamsanga n’kuitenga.

8 Tsopano mfumu ya Siriya+ inayamba kuchita nkhondo ndi Isiraeli. Chotero inakambirana ndi atumiki ake+ kuti: “Tikasonkhane pamalo akutiakuti.”+ 9 Kenako munthu wa Mulungu woona+ uja anatumiza uthenga kwa mfumu ya Isiraeli, wakuti: “Samalani kuti musadutse pamalo akutiakuti+ chifukwa Asiriya akupita kumeneko.”+ 10 Pamenepo mfumu ya Isiraeli inatumiza anthu kumalo amene munthu wa Mulungu woona uja anaiuza.+ Elisa anachenjeza+ mfumu ya Isiraeli ndipo sinapiteko. Izi zinachitika kangapo, osati kamodzi kapena kawiri kokha.

11 Choncho mfumu ya Siriya inapsa mtima kwambiri+ chifukwa cha zimenezo, moti inaitanitsa atumiki ake ndipo inawafunsa kuti: “Ndiuzeni, ndani pakati pa ife amene ali kumbali ya mfumu ya Isiraeli?”+ 12 Ndiyeno mmodzi wa atumiki ake anati: “Palibe, mbuyanga mfumu, koma mneneri Elisa+ amene ali ku Isiraeli, ndi amene amauza+ mfumu ya Isiraeli zinthu zimene inuyo mumalankhula kuchipinda kwanu.”+ 13 Choncho mfumuyo inati: “Amuna inu pitani mukaone kumene ali, kuti nditumizeko anthu akamutenge.”+ Kenako mfumuyo inauzidwa kuti: “Ali ku Dotana.”+ 14 Nthawi yomweyo mfumuyo inatumizako mahatchi, magaleta ankhondo, ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu.+ Iwo anafikako usiku ndipo anazungulira mzindawo.

15 Mtumiki+ wa munthu wa Mulungu woona atadzuka m’mawa n’kutuluka panja, anangoona kuti gulu lankhondo lazungulira mzindawo ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo. Nthawi yomweyo mtumikiyo anadandaulira mbuye wake kuti: “Kalanga ine mbuyanga!+ Titani?” 16 Koma iye anati: “Usaope,+ popeza ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.”+ 17 Kenako Elisa anayamba kupemphera+ kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso+ chonde kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa+ linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo+ oyaka moto.

18 Asiriyawo atayamba kupita kumene kunali Elisa, iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Chonde chititsani khungu mtundu uwu.” Chotero iye anawachititsa khungu+ malinga ndi mawu a Elisa. 19 Tsopano Elisa anawauza kuti: “Njira yake si imeneyi ndipo mzinda wake si umenewu. Nditsatireni, ndikulondolerani kwa munthu amene mukufuna.” Koma anawapititsa ku Samariya.+

20 Atangofika ku Samariya, Elisa anati: “Yehova, atseguleni maso anthuwa kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso awo ndipo anaona+ kuti ali pakatikati pa Samariya. 21 Mfumu ya Isiraeli itangoona anthuwo, inafunsa Elisa kuti: “Kodi ndiwaphe?+ Ndiwaphe kodi bambo?”+ 22 Koma Elisa anati: “Musawaphe. Kodi mukufuna kupha anthu amene mwawagonjetsa ndi lupanga ndi uta n’kuwagwira?+ Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa.+ Kenako apite kwa mbuye wawo.” 23 Chotero mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu ndipo anayamba kudya ndi kumwa. Atatha anawauza kuti azipita ndipo anapita kwa mbuye wawo. Kuchokera pamenepo, magulu a achifwamba+ a Asiriya sanabwerenso ku Isiraeli.

24 Pambuyo pake Beni-hadadi mfumu ya Siriya anasonkhanitsa asilikali ake onse ndipo anapita kukazungulira+ mzinda wa Samariya. 25 Patapita nthawi, mu Samariya+ munagwa njala yaikulu. Asiriyawo anapitirizabe kuzungulira mzindawo mpaka mtengo wogulira mutu wa bulu+ unafika pa ndalama 80 zasiliva, ndipo zitosi za nkhunda+ zodzaza manja awiri* mtengo wake unafika pa ndalama zisanu zasiliva. 26 Mfumu ya Isiraeli ikuyenda pamwamba pa khoma, mayi wina analankhula mokweza kwa mfumuyo kuti: “Ndithandizeni mbuyanga mfumu!”+ 27 Mfumuyo inayankha kuti: “Ngati Yehova sakukuthandiza ndiye ine ndingakuthandize ndi chiyani?+ Kodi ndingakuthandize ndi zochokera popunthira mbewu, mopondera mphesa, kapena moyengera mafuta?” 28 Ndiyeno mfumuyo inam’funsa kuti: “Vuto lako ndi lotani?” Mayiyo anayankha kuti: “Mayi uyu anandiuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye lero, ndipo mwana wanga timudya mawa.’+ 29 Choncho tinaphika+ mwana wanga n’kumudya.+ Tsiku lotsatira ndinauza mayiyu kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye.’ Koma iye anakam’bisa.”

30 Mfumuyo itamva mawu a mayiyo, nthawi yomweyo inang’amba+ zovala zake, ndipo pamene inali kuyendabe pamwamba pa khomalo, anthu anaona kuti inali itavala chiguduli* mkati. 31 Kenako inapitiriza kulankhula kuti: “Mulungu andilange mowirikiza, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati ukhalebe pa iye lero!”+

32 Tsopano Elisa anali atakhala m’nyumba mwake pamodzi ndi akulu+ pamene mfumu inatumiza mthenga kwa iye. Mthengayo asanafike, Elisa anauza akuluwo kuti: “Kodi mwaona kuti mwana wa munthu wopha anthu+ uja watumiza munthu kuti adzandidule mutu? Muonetsetse kuti mthengayo akangofika mutseke chitseko ndipo muchitsamire kuti asathe kulowa. Kodi mapazi a mbuye wake si amene akumveka+ pambuyo pakewo?” 33 Elisa ali mkati molankhula nawo, mthenga uja anafika, ndipo mfumu inati: “Tsokali lachokera kwa Yehova.+ Kodi pali chifukwa choti ndipitirizire kuyembekezera Yehova?”+

7 Tsopano Elisa anati: “Amuna inu, mverani mawu a Yehova.+ Yehova wanena kuti, ‘Mawa chapanthawi ngati ino, pachipata cha Samariya, ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya,* mtengo wake udzakhala sekeli* limodzi, ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake udzakhalanso sekeli limodzi.’”+ 2 Koma msilikali wothandiza mfumu amene anaigwira ndi dzanja lake,+ anayankha munthu wa Mulungu woonayo, kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba,+ kodi zimenezo zingachitike?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako,+ koma sudya nawo.”+

3 Ndiyeno panali anthu anayi akhate amene anali pachipata.+ Iwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi tikhalirenji pano mpaka kufa? 4 Tikati, ‘Tiyeni tilowe mumzinda,’ tikafera momwemo chifukwa muli njala.+ Tikatinso tikhale pano, tifa. Ndiye tiyeni tikalowe mumsasa wa Asiriya. Akakatisiya ndi moyo, tikhala ndi moyo, koma akakatipha, chabwino tikafa.”+ 5 Choncho ananyamuka kukungoyamba kumene kuda, n’kukalowa mumsasa wa Asiriyawo. Anakafika m’mphepete mwa msasawo ndipo anadabwa kupeza kuti munalibe aliyense.

6 Yehova anali atachititsa anthu a mumsasa wa Asiriyawo kumva+ phokoso la magaleta ankhondo, phokoso la mahatchi, ndi phokoso la gulu lalikulu la asilikali amphamvu.+ Choncho anthuwo anauzana kuti: “Taonani! Mfumu ya Isiraeli yaitanitsa mafumu a Ahiti+ ndi mafumu a Iguputo+ kuti abwere kudzamenyana nafe!” 7 Nthawi yomweyo anthuwo ananyamuka n’kuyamba kuthawa kukungoyamba kumene kuda.+ Anasiya mahema awo, mahatchi awo,+ ndi abulu awo. Msasawo anausiya mmene unalili n’kuthawa kuti apulumutse miyoyo yawo.+

8 Akhate aja atafika m’mphepete mwa msasawo, analowa m’hema mmodzi ndipo anayamba kudya ndi kumwa. Kenako anatengamo siliva, golide, ndi zovala n’kupita nazo kwina kukazibisa. Atatero anabwereranso n’kudzalowa m’hema wina ndipo anatengamonso zinthu zina n’kukazibisa.+

9 Pomalizira pake, anayamba kuuzana kuti: “Zimene tikuchitazi si zabwino. Tiyeni tikauze ena nkhani yabwinoyi!+ Tikazengereza n’kudikira mpaka kucha, tidzakhala ndi mlandu.+ Choncho tiyeni tikalowe mumzinda ndipo tikanene kunyumba ya mfumu.” 10 Chotero akhatewo anapita n’kukafuulira alonda a pachipata+ cha mzinda kuti: “Tinapita kumsasa wa Asiriya ndipo tapeza kuti kulibe aliyense. Sikukumveka mawu a munthu aliyense koma kuli mahatchi ndi abulu omangidwa ndipo mahema ali mmene analili.”+ 11 Nthawi yomweyo, alonda a pachipatawo anafuulira anthu amene anali m’nyumba ya mfumu.

12 Mfumuyo itangomva inadzuka usiku, ndipo inauza atumiki ake kuti:+ “Ndikuuzeni zimene Asiriyawa atichita.+ Iwo akudziwa bwino kuti ife tili ndi njala,+ choncho achoka mumsasamo n’kukabisala kutchire.+ Maganizo awo ndi akuti, ‘Atuluka mumzindamo ndipo tiwagwira amoyo. Kenako ifeyo tikalowa mumzindamo.’” 13 Ndiyeno mtumiki mmodzi wa mfumu anayankha kuti: “Uzani anthu atenge mahatchi asanu pa mahatchi amene atsala mumzinda ndipo muwatume kuti akaone. Anthuwo n’chimodzimodzi ndi gulu lonse la Aisiraeli amene atsala mumzindamu,+ ndiponso n’chimodzimodzi ndi gulu lonse la Aisiraeli amene afa.”+ 14 Choncho iwo anatenga magaleta awiri ndi mahatchi, ndipo mfumu inawatuma kumsasa wa Asiriya ndi kuwauza kuti: “Pitani mukaone.” 15 Anthuwo anatsatira Asiriyawo mpaka kukafika ku Yorodano, ndipo m’njira monsemo munali zovala ndi ziwiya+ zimene Asiriyawo anataya pothawa.+ Kenako anthuwo anabwerera n’kukanena kwa mfumu.

16 Tsopano anthu anapita kukafunkha+ msasa wa Asiriya. Choncho ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake unafika pa sekeli imodzi, ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake unafikanso pa sekeli imodzi, mogwirizana ndi mawu+ a Yehova. 17 Mfumu inaika msilikali woithandiza amene anaigwira+ ndi dzanja uja kuti akhale woyang’anira pachipata. Koma anthu anam’pondaponda+ pachipatapo moti anafa, monga mmene munthu wa Mulungu woona uja ananenera,+ pamene mfumu inabwera kwa iye. 18 Chotero zinachitikadi monga mmene munthu wa Mulungu woona uja ananenera kwa mfumu, kuti: “Balere wokwana miyezo iwiri ya seya mtengo wake udzafika pa sekeli imodzi, ndipo ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake udzafikanso pa sekeli imodzi mawa, pa nthawi ngati ino pachipata cha Samariya.”+ 19 Koma msilikali wothandiza mfumu uja anamuyankha munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba, kodi mawu anuwa angakwaniritsidwe?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako, koma sudya nawo.”+ 20 Choncho zinam’chitikiradi motero+ pamene anthu anam’pondaponda+ pachipata mpaka kufa.

8 Tsopano Elisa anauza mayi amene anamuukitsira mwana uja,+ kuti: “Nyamuka, iwe ndi banja lako, ukakhale monga mlendo kulikonse kumene ungakakhale,+ chifukwa Yehova abweretsa njala.+ Njalayo idzatenga zaka 7.”+ 2 Choncho, mayiyo ndi banja lake+ ananyamuka+ n’kupita kukakhala monga mlendo m’dziko la Afilisiti+ kwa zaka 7, mogwirizana ndi mawu a munthu wa Mulungu woona.

3 Zaka 7 zija zitatha, mayiyo anabwerera kuchokera kudziko la Afilisiti n’kupita kukadandaulira mfumu+ kuti imupatse nyumba yake ndi munda wake. 4 Pa nthawiyo, mfumu inali ikulankhula ndi Gehazi+ mtumiki wa munthu wa Mulungu woona, kuti: “Ndifotokozere zinthu zonse zazikulu zimene Elisa wachita.”+ 5 Gehazi akufotokozera mfumuyo mmene Elisa anaukitsira munthu wakufa,+ anangomva mayi wa mwana amene anaukitsidwayo akudandaulira mfumu kuti imupatse nyumba yake ndi munda wake.+ Nthawi yomweyo Gehazi anati: “Mbuye wanga+ mfumu, mayiyo ndi uyu, ndiponso mwana wake amene Elisa anamuukitsa uja ndi uyu.” 6 Ndiyeno mfumuyo inapempha mayiyo kuti aifotokozere nkhani yonse,+ ndipo mayiyo anafotokozadi. Kenako mfumuyo inauza nduna ya panyumba yake+ kuti: “Mayiyu um’bwezere zinthu zake zonse, ndipo umupatse ndalama zimene akanapeza pa zokolola za kumunda kwake pa nthawi yonse imene anachokapo kufikira lero.”+

7 Kenako Elisa anapita ku Damasiko.+ Kumeneko Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya inali kudwala. Choncho mfumuyo inauzidwa kuti: “Munthu wa Mulungu woona uja+ wafika kuno.” 8 Mfumuyo itamva zimenezi, inauza Hazaeli kuti:+ “Tenga mphatso,+ upite kukakumana ndi munthu wa Mulungu woonayo. Ukafunsire+ mawu a Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’” 9 Choncho Hazaeli anatenga mphatsozo n’kupita kukakumana naye. Anatenga chinthu chilichonse chabwino cha m’Damasiko. Mphatsozo anazinyamula pangamira zokwana 40. Atafika, anaima pamaso pa Elisa n’kunena kuti: “Mwana wanu+ Beni-hadadi mfumu ya Siriya wandituma kudzakufunsani kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’” 10 Ndiyeno Elisa anayankha Hazaeli kuti: “Pita ukamuuze kuti, ‘Muchira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa+ kuti afa ndithu.”+ 11 Pamenepo Elisa anayang’anitsitsa Hazaeli kuti dwii! mpaka Hazaeliyo anachita manyazi. Kenako munthu wa Mulungu woonayo anayamba kulira.+ 12 Hazaeli ataona zimenezi anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira mbuyanga?” Elisa anayankha kuti: “Chifukwa ndikudziwa bwino zoipa+ zimene iweyo udzachitire ana a Isiraeli. Malo awo otetezedwa udzawatentha ndi moto, amuna ochita kusankhidwa pakati pawo udzawapha ndi lupanga, ana awo aang’ono udzawaphwanyaphwanya,+ ndipo akazi awo apakati udzawatumbula.”+ 13 Hazaeli atamva mawu amenewa, anati: “Ndine ndani ine mtumiki wanu, galu ngati ine,+ kuti ndichite zinthu zazikulu ngati zimenezi?” Koma Elisa anati: “Yehova wandionetsa iweyo utakhala mfumu ya Siriya.”+

14 Pambuyo pake Hazaeli anachoka kwa Elisa ndipo anapita kwa mbuye wake. Ndiyeno mbuye wakeyo anam’funsa kuti: “Kodi Elisa wakuuza kuti chiyani?” Hazaeli anayankha kuti: “Wandiuza kuti, ‘Muchira ndithu.’”+ 15 Tsiku lotsatira, Hazaeli anatenga chofunda n’kuchiviika m’madzi. Kenako anaphimba nacho mfumuyo kumaso+ moti inamwalira,+ ndipo Hazaeli+ anayamba kulamulira m’malo mwake.

16 M’chaka chachisanu cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, pamene Yehosafati anali mfumu ya Yuda, Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, anakhala mfumu. 17 Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.+ 18 Iye anayenda m’njira ya mafumu a Isiraeli+ monga mmene ankachitira a m’nyumba ya Ahabu,+ chifukwa anakwatira+ mwana wa Ahabu. Choncho iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. 19 Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda+ chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ pakuti anamulonjeza kuti adzam’patsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.

20 M’masiku a Yehoramu, Aedomu+ anagalukira Yuda. Iwo anachoka m’manja mwa Yuda n’kusankha mfumu+ yoti iziwalamulira. 21 Choncho Yehoramu anapita ku Zairi usiku pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku n’kukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta, ndipo anthu ena onse anathawira kumahema awo. 22 Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Inalinso nthawi imeneyi pamene Libina+ anagalukira Yuda.

23 Nkhani zina zokhudza Yehoramu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 24 Pomalizira pake, Yehoramu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Kenako mwana wake Ahaziya+ anayamba kulamulira m’malo mwake.

25 M’chaka cha 12 cha Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anakhala mfumu.+ 26 Ahaziya anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi.+ Mayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri+ mfumu ya Isiraeli. 27 Iye anayenda m’njira ya anthu a m’nyumba ya Ahabu,+ ndipo anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ monga mmene anachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa anali wachibale wa nyumba ya Ahabu.+ 28 Chotero iye anapita ku nkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Koma Asiriyawo anakatha+ Yehoramu. 29 Choncho mfumu Yehoramu+ inabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti ikachire zilonda zimene Asiriya anaivulaza ku Rama,* pamene inali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Ahaziya+ mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.

9 Mneneri Elisa anaitana mmodzi wa ana+ a aneneri n’kumuuza kuti: “Konzeka,*+ nyamula botolo ladothi+ la mafutali m’manja mwako, upite ku Ramoti-giliyadi.+ 2 Ukakalowa mumzindawo, ukafufuze Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi. Ukakam’peza, ukamutenge pakati pa abale ake ndipo ukalowe naye m’chipinda chamkati.+ 3 Ndiyeno ukatenge botolo ladothi la mafutali n’kumuthira pamutu,+ ndipo ukanene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza+ iwe kukhala mfumu+ ya Isiraeli.”’ Ukakatero, ukatsegule chitseko ndi kuthawa, usakachedwe.”

4 Ndiyeno mtumiki wa mneneriyo ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi. 5 Atalowa mumzindawo, anapeza akuluakulu a asilikali atakhalakhala. Kenako iye anati: “Ndili nanu mawu inu+ mkulu wa asilikali.” Ndiyeno Yehu anati: “Ndani kwenikweni pakati pa tonsefe?” Iye anayankha kuti: “Inuyo mkulu wa asilikali.” 6 Choncho Yehu ananyamuka n’kulowa m’nyumba. Mmenemo mtumiki wa mneneri uja anatenga mafuta aja n’kumuthira pamutu. Kenako anamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikukudzoza iwe kukhala mfumu+ ya anthu a Yehova,+ kutanthauza Aisiraeli. 7 Ukaphe anthu a m’nyumba ya mbuye wako Ahabu, kuti ine ndibwezere+ magazi a atumiki anga aneneri ndiponso magazi a atumiki onse a Yehova amene Yezebeli anapha.+ 8 Nyumba yonse ya Ahabu+ ifafanizidwe. Ine ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’banja la Ahabu, ngakhale aliyense wonyozeka ndi wopanda pake+ mu Isiraeli. 9 Ndidzachititsa nyumba ya Ahabu kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati, ndiponso ngati nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya. 10 Yezebeli adzadyedwa ndi agalu+ m’munda wa ku Yezereeli, ndipo palibe amene adzamuike m’manda.’” Mtumikiyo atamaliza kunena zimenezi, anatsegula chitseko n’kuthawa.+

11 Ndiyeno Yehu anatuluka n’kupita kwa atumiki a mbuye wake. Atumikiwo anayamba kum’funsa kuti: “Zili bwino kodi?+ Nanga munthu wamisalayu+ amadzatani kwa iwe?” Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo mukum’dziwa bwino munthuyu ndiponso zonena zake.” 12 Koma iwo anati: “Ayi ukunama! Tiuze zoona.” Pamenepo Yehu anati: “Munthu uja anandiuza zakutizakuti, ndipo anati, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza iwe kukhala mfumu ya Isiraeli.”’”+ 13 Anthuwo atamva zimenezi, msangamsanga aliyense anavula malaya ake+ n’kumuyalira pamasitepe popanda kanthu. Kenako anayamba kuliza malipenga,+ ndipo anali kunena kuti: “Yehu wakhala mfumu!”+ 14 Tsopano Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi,+ anayamba kukonzera Yehoramu chiwembu.+

Pa nthawiyi n’kuti Yehoramu akulondera Ramoti-giliyadi+ pamodzi ndi Aisiraeli onse, chifukwa cha Hazaeli+ mfumu ya Siriya. 15 Pambuyo pake, mfumu Yehoramu+ inabwerera ku Yezereeli+ kukachira zilonda zake zimene Asiriya anaivulaza pamene inali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+

Kenako Yehu anati: “Ngati mukugwirizana nazo,+ musalole aliyense kuthawa kutuluka mumzinda uno kuti akanene ku Yezereeli.” 16 Tsopano Yehu anakwera galeta ulendo wa ku Yezereeli popeza Yehoramu anali chigonere kumeneko. Ahaziya+ mfumu ya Yuda anali atapita ku Yezereeli komweko kukaona Yehoramu. 17 Ku Yezereeliko,+ mlonda+ amene anaimirira pansanja+ anaona gulu lankhondo la Yehu likubwera mwaliwiro. Nthawi yomweyo mlondayo anati: “Ndikuona gulu la amuna likubwera mwaliwiro.” Pamenepo Yehoramu anati: “Uza munthu wokwera hatchi kuti apite kukakumana nawo. Akawafunse kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ 18 Chotero munthu wokwera pahatchiyo anapitadi kukakumana ndi Yehu, n’kunena kuti, “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendere’ iweyo? Tiye zinditsatira!”

Ndiyeno mlonda+ wa pansanja uja anati: “Munthu wauthenga tinam’tuma uja wakumana nawo koma sakubwerera.” 19 Tsopano anatumiza munthu wina wachiwiri wokwera pahatchi. Iyenso atafika anati: “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendere’ iweyo? Tiye zinditsatira!”

20 Mlonda wa pansanja uja ananenanso kuti: “Munthu tamutuma ujanso wakumana nawo, koma sakubwerera. Ndipo mmene anthuwo akuthamangira, akuthamanga ngati Yehu+ mdzukulu wa Nimusi,+ pakuti iye amathamangitsa galeta ngati wamisala.”+ 21 Yehoramu atamva zimenezi, anati: “Mangirirani mahatchi kugaleta!”+ Chotero anamangiriradi mahatchi kugaleta lake lankhondo. Ndiyeno Yehoramu mfumu ya Isiraeli ndi Ahaziya+ mfumu ya Yuda, ananyamuka aliyense pagaleta lake lankhondo, kupita kukakumana ndi Yehu, ndipo anakumana naye pamunda wa Naboti+ Myezereeli.

22 Yehoramu atangoona Yehu, nthawi yomweyo anam’funsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Koma Yehu anayankha kuti: “Mtendere ungakhalepo bwanji+ pali dama la Yezebeli+ mayi ako ndi amatsenga ake ambirimbiri?”+ 23 Ndiyeno Yehoramu anatembenuza galeta lake kuti azithawa, ndipo anauza Ahaziya kuti: “Ahaziya, anthuwa atikonzera chiwembu!”+ 24 Pamenepo Yehu anakoka uta+ wake n’kulasa Yehoramu kumsana pakati pamapewa, mpaka muviwo unatulukira pamtima pake, moti Yehoramu anagwa m’galeta lake lankhondo.+ 25 Kenako Yehu anauza msilikali wake womuthandiza pagaleta+ dzina lake Bidikara, kuti: “Munyamule, umuponye m’munda wa Naboti Myezereeli.+ Kumbukira kuti iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu bambo ake, aliyense atakwera pagaleta lake la mahatchi awiri, pa nthawi imene Yehova anam’temberera+ kuti: 26 ‘“Ndithu magazi+ a Naboti ndi magazi a ana ake+ amene ndawaona dzulo,” watero Yehova, “ndidzawabwezera+ pa iwe ndithu m’munda uwu,” Yehova watero.’ Choncho munyamule, umuponye m’mundamo mogwirizana ndi mawu a Yehova.”+

27 Ahaziya+ mfumu ya Yuda, anaona zonsezo moti anayamba kuthawa kudzera njira ya kumunda.*+ (Pambuyo pake Yehu anayamba kum’tsatira, ndipo anati: “Ameneyonso m’kantheni!” Choncho anam’kanthadi ali m’galeta lake pamene anali kuthawira ku Guru, kufupi ndi ku Ibuleamu.+ Iye anapitirizabe kuthawa mpaka ku Megido+ kumene anakafera.+ 28 Kenako atumiki ake anamunyamula m’galeta ndi kupita naye ku Yerusalemu kumene anakamuika m’manda ake pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ 29 Ahaziya+ anakhala mfumu ya Yuda m’chaka cha 11 cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu.)

30 Kenako Yehu anafika ku Yezereeli,+ ndipo Yezebeli+ anamva zimenezo. Yezebeliyo anadzikongoletsa podzipaka utoto+ wakuda m’maso mwake n’kukongoletsanso tsitsi lake mochititsa kaso.+ Atatero anakaima pawindo n’kumayang’ana kunja.+ 31 Ndiyeno Yehu anafika pachipata, ndipo Yezebeli anati: “Kodi Zimiri+ amene anapha mbuye wake, zinthu zinamuyendera bwino?” 32 Yehu atamva mawu amenewa, anakweza maso kuyang’ana pawindopo, n’kufunsa kuti: “Ndani ali kumbali yanga? Ndani?”+ Nthawi yomweyo nduna ziwiri kapena zitatu za panyumba ya mfumu+ zinasuzumira pansi kuyang’ana Yehu. 33 Ndiyeno Yehu anati: “M’ponyeni+ pansi Yezebeliyo!” Iwo anam’ponyadi pansi, ndipo magazi ake ena anamwazika n’kuwaza khoma ndi mahatchi. Kenako Yehu anam’pondaponda+ ndi mahatchi ake. 34 Atatero, analowa m’nyumba ndipo anayamba kudya ndi kumwa, kenako anati: “Amuna inu, m’samaleni munthu wotembereredwayu.+ M’tengeni mukamuike m’manda, popeza ndi mwana wa mfumu.”+ 35 Atapita kuti akam’tenge kukamuika m’manda, sanapezepo chilichonse. Iwo anangopezapo mutu, mapazi, ndi zikhatho zake. + 36 Anthuwo atabwerera kwa Yehu kukamuuza, iye anati: “Amenewo ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera+ mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, kuti, ‘M’munda wa ku Yezereeli, agalu adzadya mnofu wa Yezebeli.+ 37 Ndipo mtembo wa Yezebeli, ndithu udzasanduka manyowa+ m’munda wa ku Yezereeli kuti anthu asadzanene kuti: “Uyu ndi Yezebeli.”’”+

10 Ku Samariya+ kunali ana aamuna a Ahabu okwanira 70.+ Chotero Yehu analemba makalata n’kuwatumiza kwa atsogoleri+ a ku Yezereeli, kwa akuluakulu,+ ndi kwa anthu amene ankasamalira ana a Ahabu ku Samariya. M’makalatamo analembamo kuti: 2 “Inu muli ndi ana aamuna a mbuye wanu, magaleta ankhondo ndi mahatchi,+ ndiponso mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndi zida zankhondo. Choncho mukangolandira kalatayi, 3 musankhe mwana mmodzi woyenera ndi wolungama pakati pa ana aamuna a mbuye wanu, n’kumuika pampando wachifumu wa bambo ake.+ Kenako mumenyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.”

4 Iwo atalandira makalatawo anachita mantha kwambiri, ndipo anayamba kunena kuti: “Mafumu+ awiri sanathe kulimbana naye, nanga ifeyo tingalimbane naye bwanji?”+ 5 Chotero, amene anali kuyang’anira nyumba ya mfumu, ndi amene anali kuyang’anira mzinda, ndiponso akuluakulu komanso amene ankasamalira+ Ahabu, anatumiza uthenga kwa Yehu, wakuti: “Ife ndife atumiki anu, ndipo tichita chilichonse chimene mungatiuze. Sitisankha munthu aliyense kuti akhale mfumu yathu. Inuyo chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino.”

6 Pamenepo Yehu anawalemberanso kalata yachiwiri kuti: “Ngati muli kumbali yanga+ ndipo ngati muzimvera mawu anga, dulani mitu ya ana aamuna+ a mbuye wanu, ndipo mawa nthawi ngati yomwe ino mubwere nayo kwa ine ku Yezereeli.”+

Ana aamuna a mfumuwo, omwe analipo 70, anali ndi akuluakulu a mumzindawo omwe anali kuwasamalira. 7 Anthuwo atangolandira kalatayo, anatenga ana aamuna a mfumu okwanira 70 aja+ n’kuwapha. Kenako anatenga mitu yawo n’kuiika m’madengu, ndipo anaitumiza kwa Yehu ku Yezereeli. 8 Ndiyeno kunabwera mthenga+ kudzauza Yehu kuti: “Mitu ya ana+ a mfumu ija abwera nayo.” Pamenepo Yehu anati: “Kaiunjikeni milu iwiri pachipata, ndipo ikhale pamenepo kufikira m’mawa.”+ 9 M’mawa kutacha, Yehu anapita kukaima pamaso pa anthu onse. Kenako ananena kuti: “Anthu inu ndinu olungama.+ Ine ndinachitira chiwembu+ mbuye wanga, ndipo ndamupha,+ koma ndani wapha anthu onsewa? 10 Tsopano dziwani kuti mawu onse a Yehova otsutsa nyumba ya Ahabu+ amene Yehova analankhula, adzakwaniritsidwa.+ Yehova wachita zimene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya.”+ 11 Kuwonjezera apo, Yehu anapitiriza kupha onse a m’nyumba ya Ahabu amene anatsala ku Yezereeli, amuna ake onse olemekezeka,+ anzake, ndi ansembe ake,+ mpaka onse anatha.+

12 Kenako Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Ali pa ulendowo, anafika panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. 13 Pamenepo Yehu anakumana ndi abale+ ake a Ahaziya+ mfumu ya Yuda. Atawafunsa kuti, “Ndinu ndani?” iwo anayankha kuti: “Ndife abale ake a Ahaziya. Tikupita kukaona ngati ana a mfumu ndi ana a mfumukazi ali bwino.” 14 Nthawi yomweyo Yehu anati: “Amuna inu, agwireni amoyo+ anthuwa!” Choncho anawagwiradi amoyo n’kukawaphera pachitsime cha panyumba imene abusa ankameteramo ubweya wa nkhosa. Anawapha onse 42 ndipo palibe amene anamusiya ndi moyo.+

15 Yehu atachoka pamenepo, anakumana ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu+ akubwera kudzakumana naye. Atamudalitsa,+ anam’funsa kuti: “Kodi mtima wako ndi wogwirizana ndi ine mopanda chinyengo, monga momwe mtima wanga ulili ndi mtima wako?”+

Yehonadabu anayankha kuti: “Inde, ndi wotero.”

Ndiyeno Yehu anati: “Ngati ndi wotero, ndipatse dzanja lako.”

Choncho Yehonadabu anapereka dzanja lake, ndipo Yehu anamukweza m’galeta lake.+ 16 Kenako anamuuza kuti: “Tiye tipitire limodzi ukaone kuti sindilekerera zoti anthu azipikisana+ ndi Yehova.” Chotero Yehonadabu anapita limodzi ndi anthuwo atakwera m’galeta lankhondo la Yehu. 17 Pomalizira pake Yehu anafika ku Samariya. Kumeneko, iye anapha anthu onse a m’nyumba ya Ahabu amene anatsala ku Samariya, mpaka anawatha onse,+ mogwirizana ndi mawu a Yehova amene anauza Eliya.+

18 Komanso Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi n’kuwauza kuti: “Ahabu anali kupembedza Baala pang’ono,+ koma Yehu apembedza Baala kwambiri. 19 Tsopano itanani aneneri+ onse a Baala, olambira ake onse,+ ndi ansembe ake+ onse kuti abwere kwa ine. Pasapezeke aliyense wotsala chifukwa ndakonza nsembe yaikulu yoti ndipereke kwa Baala. Aliyense amene palibe sakhala ndi moyo.” Koma Yehu anawapusitsa+ n’cholinga choti awononge anthu olambira Baala.

20 Ndiyeno Yehu anati: “Lengezani* kuti kuli msonkhano wapadera wa Baala.” Choncho analengezadi. 21 Kenako Yehu anatumiza uthenga mu Isiraeli+ yense, moti olambira onse a Baala+ anabwera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene sanabwere. Iwo analowa m’kachisi wa Baala ndipo kachisiyo anadzaza kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. 22 Tsopano iye anauza munthu amene anali kuyang’anira chipinda chosungira zovala kuti: “Tulutsa zovala zoti olambira onse a Baala avale.” Choncho iye anawatulutsiradi zovalazo. 23 Kenako Yehu ndi Yehonadabu+ mwana wa Rekabu analowa m’kachisi wa Baala. Tsopano Yehu anauza olambira a Baala kuti: “Fufuzani mosamala, ndipo muonetsetse kuti muno musakhale wolambira wa Yehova aliyense, koma olambira a Baala okha.”+ 24 Pomaliza pake, iwo anabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina. Yehu anaika amuna 80 panja oti amuthandize ndipo anawauza kuti: “Aliyense amene athawitse munthu pa anthu amene ndikuwapereka m’manja mwanu, moyo wake ulowa m’malo mwa munthuyo.”+

25 Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, nthawi yomweyo anauza asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta kuti: “Lowani, apheni! Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotuluka panja.”+ Atamva zimenezi, asilikali ake othamanga ndi othandiza pamagaleta+ aja anayamba kupha anthuwo ndi lupanga n’kumaponyera mitembo yawo panja. Anakafika mpaka m’chipinda chamkati mwa kachisiyo chotchedwa mzinda wa Baala. 26 Kenako anatulutsa zipilala zopatulika+ za m’kachisi wa Baala n’kuzitentha+ zonse. 27 Anagwetsanso chipilala chopatulika cha Baala+ ndi kachisi wa Baala,+ ndipo malowo anawasandutsa zimbudzi+ mpaka lero.

28 Chotero Yehu anachotsa Baala mu Isiraeli. 29 Kungoti iye sanasiye kutsatira machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ Machimo ake anali kulambira ana a ng’ombe agolide.+ Mmodzi wa ana a ng’ombe agolidewo anali ku Beteli, ndipo wina ku Dani.+ 30 Chotero Yehova anauza Yehu kuti: “Pa chifukwa chakuti wachita bwino, mwa kuchita zoyenera pamaso panga,+ ndiponso wachitira nyumba ya Ahabu+ mogwirizana ndi zonse za mumtima mwanga, ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.”+ 31 Koma Yehu sanayesetse kuyenda motsatira malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ Sanapatuke pa machimo a Yerobowamu amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+

32 M’masiku amenewo, Yehova anayamba kulanda dziko la Isiraeli pang’ono ndi pang’ono, ndipo Hazaeli+ anapitiriza kupha anthu m’madera onse a dziko la Isiraeli. 33 Anayambira ku Yorodano chakotulukira dzuwa, dziko lonse la Giliyadi,+ Agadi,+ Arubeni+ ndi Amanase,+ kuyambira ku Aroweli+ yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni, ngakhalenso Giliyadi ndi Basana.+

34 Nkhani zina zokhudza Yehu ndi zonse zimene anachita, ndiponso zochita zake zonse zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 35 Pomalizira pake Yehu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda ku Samariya. Kenako Yehoahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 36 Masiku amene Yehu analamulira Isiraeli ku Samariya, anakwana zaka 28.

11 Tsopano Ataliya,+ mayi wa Ahaziya+ ataona kuti mwana wake wafa, anapha ana onse achifumu.+ 2 Koma Yehoseba+ mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa+ m’chipinda chamkati chogona kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe. 3 Anapitiriza kubisidwa m’nyumba ya Yehova zaka 6, pamene Ataliya anali kulamulira dzikolo.+

4 M’chaka cha 7, Yehoyada+ anatumiza uthenga kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu Achikariya,+ ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 othamanga.+ Anawaitanitsa kuti abwere kwa iye kunyumba ya Yehova ndipo anachita nawo pangano+ n’kuwalumbiritsa+ kunyumba ya Yehova. Kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja. 5 Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Gawo limodzi mwa magawo atatu a inu lidzabwere pa tsiku la sabata kudzalondera nyumba ya mfumu mosamala.+ 6 Gawo lina limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata+ chotchedwa Maziko, ndipo gawo linanso limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata kumbuyo kwa asilikali othamanga. Muzidzasinthana kulondera mosamala nyumbayo.+ 7 Magulu awiri a inu amene adzatuluke pa sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu. 8 Mudzaizungulire mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga zida zake m’manja, ndipo aliyense wolowa pakati pa mizere ya anthu adzaphedwe. Muzidzakhala limodzi ndi mfumuyo ikamatuluka ndiponso ikamalowa.”

9 Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata,+ pamodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata, n’kupita kwa wansembe Yehoyada. 10 Tsopano wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira za Mfumu Davide, zomwe zinali m’nyumba ya Yehova.+ 11 Asilikali othamanga+ anaimirira, aliyense atatenga zida zake m’manja, kuyambira kumbali yakumanja* ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere* ya nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 12 Kenako anatulutsa mwana+ wa mfumu uja. Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu+ n’kumudzoza.+ Ndiyeno anayamba kuwomba m’manja+ n’kumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+

13 Ataliya atamva anthu akuchita phokoso komanso akuthamanga, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+ 14 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala+ malinga ndi mwambo wawo. Anaonanso atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba malipenga. Nthawi yomweyo Ataliya+ anang’amba zovala zake n’kuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+ 15 Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa,+ kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu! Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!”+ Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Muonetsetse kuti asaphedwere m’nyumba ya Yehova.” 16 Choncho anamugwira n’kumutulutsira pakhomo la kunyumba ya mfumu+ lolowera mahatchi,+ ndipo anam’phera pamenepo.+

17 Kenako Yehoyada anachita pangano+ pakati pa Yehova,+ mfumu,+ ndi anthu, kuti anthuwo azisonyeza kuti ndi anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+ 18 Pambuyo pake, anthu onse a m’dzikolo anapita kukachisi wa Baala n’kukagwetsa maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha patsogolo pa maguwa ansembewo.+

Kenako wansembe Yehoyada anaika anthu kuti aziyang’anira nyumba ya Yehova.+ 19 Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100, asilikali olondera mfumu Achikariya,+ asilikali othamanga,+ ndi anthu onse a m’dzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anadzera njira ya pachipata+ cha asilikali othamanga, mpaka anafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu+ wa mafumu. 20 Anthu onse a m’dzikolo anapitiriza kusangalala,+ ndipo mumzindawo munali bata. Ataliya anali atamupha ndi lupanga panyumba ya mfumu.+

21 Yehoasi+ anali ndi zaka 7 pamene anayamba kulamulira.+

12 M’chaka cha 7 cha Yehu,+ Yehoasi+ anakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 40. Mayi ake anali a ku Beere-seba ndipo dzina lawo linali Zibiya. 2 Yehoasi anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova, masiku onse amene wansembe Yehoyada anali kumulangiza.+ 3 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.

4 Tsopano Yehoasi anauza ansembe kuti:+ “Ndalama zonse zimene anthu akubweretsa kunyumba ya Yehova+ za zopereka zopatulika,+ kutanthauza ndalama za msonkho zimene munthu aliyense akupereka,+ ndalama zoperekedwa ndi anthu amene achita chowinda,+ ndiponso ndalama zonse zimene munthu aliyense watsimikiza mumtima mwake kuti abweretse kunyumba ya Yehova,+ 5 wansembe aliyense atenge ndalama zimenezi kwa anthu owadziwa,+ ndipo anthuwo kumbali yawo akonze ming’alu ya nyumbayo paliponse pamene pali mng’alu.”+

6 Koma pofika m’chaka cha 23 cha Mfumu Yehoasi, ansembe anali asanakonzebe ming’alu ya nyumbayo.+ 7 Chotero Mfumu Yehoasi+ anaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena n’kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simukukonza ming’alu ya nyumbayi? Tsopano musatengenso ndalama zina kwa anthu owadziwa, koma muzipereke kuti akonzere ming’alu ya nyumbayi.”+ 8 Pamenepo ansembewo anavomera kuti satenganso ndalama kwa anthu, ndipo sakonza ming’alu ya nyumbayo.

9 Tsopano wansembe Yehoyada anatenga bokosi+ n’kuboola kachibowo pachivundikiro chake. Kenako anaika bokosilo pambali pa guwa lansembe kumanja, munthu akamalowa m’nyumba ya Yehova. Ansembe omwe anali alonda a pakhomo+ anaika m’bokosilo ndalama zonse+ zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Yehova. 10 Akangoona kuti m’bokosilo muli ndalama zambiri, mlembi+ wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera n’kuwerenga ndi kumanga pamodzi ndalama zimene zinali kupezeka panyumba ya Yehova.+ 11 Iwo ankapereka ndalama zimene awerengazo kwa anthu ogwira ntchito+ amene anaikidwa panyumba ya Yehova. Anthu ogwira ntchitowo ankagwiritsa ntchito ndalamazo polipira amisiri a matabwa, omanga amene anali kugwira ntchito panyumba ya Yehovayo, 12 amisiri omanga ndi miyala, ndi anthu osema miyala.+ Ndalamazo anaguliranso matabwa ndi miyala yosema yokonzera ming’alu ya nyumba ya Yehova ndiponso analipirira zonse zimene anagwiritsa ntchito pokonza nyumbayo.

13 Koma sanapange mabeseni asiliva, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ malipenga,+ ndi ziwiya zilizonse zagolide kapena zasiliva za m’nyumba ya Yehova kuchokera pa ndalama zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Yehova,+ 14 chifukwa ankapereka ndalamazo kwa anthu ogwira ntchitoyo, ndipo anthuwo anakonza nyumba ya Yehova ndi ndalamazo.+ 15 Amuna amene ankapatsidwa ndalama kuti azipereke kwa anthu ogwira ntchito,+ sankafunsidwa+ mmene ayendetsera ndalamazo chifukwa ankagwira ntchito mokhulupirika.+ 16 Ndalama za nsembe za kupalamula ndi ndalama za nsembe zamachimo+ sanali kuzibweretsa kuti adzazigwiritse ntchito yokonzetsera nyumba ya Yehova, choncho zinakhala za ansembe.+

17 Panthawi imeneyo Hazaeli+ mfumu ya Siriya anapita kukamenyana ndi mzinda wa Gati+ n’kuulanda. Kenako Hazaeli anatsimikiza zopita*+ kukaukira Yerusalemu.+ 18 Pamenepo Yehoasi mfumu ya Yuda anatenga zopereka zonse zopatulika+ zimene Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya makolo ake, mafumu a Yuda anaziyeretsa. Anatenganso zopereka za iyeyo zopatulika, ndi golide yense yemwe anali mosungira chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi cha m’nyumba ya mfumu n’kutumiza+ zonsezi kwa Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Hazaeli anabwerera osaukira Yerusalemu.

19 Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zonse zimene anachita zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 20 Koma atumiki+ a Yehoasi anagwirizana zom’chitira chiwembu+ ndipo anamupha panyumba+ ya Chimulu cha Dothi*+ panjira yotsetserekera ku Sila. 21 Atumiki ake amene anamupha anali Yozakara+ mwana wa Simeyati ndi Yehozabadi mwana wa Someri. Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide pamodzi ndi makolo ake, ndipo Amaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

13 M’chaka cha 23 cha Yehoasi+ mwana wa Ahaziya+ mfumu ya Yuda, Yehoahazi+ mwana wa Yehu+ anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya, kwa zaka 17. 2 Yehoahazi anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda motsatira tchimo la Yerobowamu+ mwana wa Nebati, limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+ Iye sanapatuke pa tchimolo. 3 Choncho mkwiyo wa Yehova+ unawayakira Aisiraeli, moti nthawi zonse ankawapereka m’manja mwa Hazaeli+ mfumu ya Siriya ndi m’manja mwa Beni-hadadi+ mwana wa Hazaeli.

4 Patapita nthawi Yehoahazi anakhazika pansi+ mtima wa Yehova, kotero kuti Yehova anamumvera,+ popeza anaona kuponderezedwa kwa Aisiraeli,+ chifukwa mfumu ya Siriya inali kuwapondereza.+ 5 Chotero Yehova anapatsa Aisiraeli mpulumutsi,+ moti anachoka m’manja mwa Siriya. Kenako ana a Isiraeli anayamba kukhala m’nyumba zawo ngati kale.+ 6 (Koma sanasiye tchimo la nyumba ya Yerobowamu limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+ Anayenda m’tchimolo,+ ndipo mzati wopatulika+ unali ulipobe ku Samariya.) 7 Yehoahazi sanatsale ndi anthu alionse kupatulapo amuna 50 okwera pamahatchi, magaleta 10, ndi asilikali 10,000 oyenda pansi,+ chifukwa mfumu ya Siriya inawawononga+ ndi kuwapondaponda ngati fumbi la popunthira mbewu.+

8 Nkhani zina zokhudza Yehoahazi ndi zonse zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 9 Pomalizira pake Yehoahazi anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda ku Samariya.+ Kenako Yehoasi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

10 M’chaka cha 37 cha Yehoasi+ mfumu ya Yuda, Yehoasi mwana wa Yehoahazi anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 16. 11 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo onse a Yerobowamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli,+ koma anayenda m’machimowo.

12 Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zonse zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, komanso momwe anamenyanirana+ ndi Amaziya mfumu ya Yuda, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 13 Pomalizira pake Yehoasi anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo Yerobowamu*+ anakhala pampando wake wachifumu. Kenako Yehoasi anaikidwa m’manda ku Samariya pamodzi ndi mafumu a Isiraeli.+

14 Tsopano Elisa+ anadwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo.+ Choncho Yehoasi mfumu ya Isiraeli anapita kwa iye n’kuyamba kulira atam’kumbatira n’kumati: “Bambo anga,+ bambo anga! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera pamahatchi ake!”+ 15 Ndiyeno Elisa anauza Yehoasi kuti: “Tengani uta ndi mivi.” Choncho iye anatenga uta ndi miviyo. 16 Kenako iye anauza mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Gwirani utawo.” Mfumuyo inaugwiradi, ndipo Elisa anaika manja ake pamanja+ a mfumuyo. 17 Kenako Elisa anati: “Tsegulani windo lakum’mawa.” Iye analitsegula. Ndiyeno Elisa anati: “Ponyani muviwo!” Choncho iye anauponya. Tsopano Elisa anati: “Muvi wa Yehova wopulumutsa! Muvi wopulumutsa+ kwa Asiriya! Ndithu mudzapha Asiriya ku Afeki+ mpaka kuwamaliza.”

18 Ananenanso kuti: “Tengani miviyo.” Pamenepo iye anaitenga. Ndiyeno Elisa anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Lasani pansi ndi miviyo.” Mfumuyo inalasa katatu n’kusiya.+ 19 Munthu wa Mulungu woonayo+ anakwiyira mfumuyo kwambiri, ndipo anati: “Mukanalasa maulendo asanu kapena maulendo 6! Mukanatero mukanaphadi Asiriya mpaka kuwamaliza, koma tsopano mudzawagonjetsa katatu kokha.”+

20 Pambuyo pa zimenezi Elisa anamwalira ndipo anamuika m’manda.+ Tsopano panali magulu a achifwamba+ achimowabu+ amene ankabwera m’dzikolo kumayambiriro kwa chaka chilichonse. 21 Tsiku lina pamene anthu anali kuika munthu m’manda, anaona gulu la achifwamba. Nthawi yomweyo iwo anaponya mtembo wa munthuyo m’manda a Elisa n’kuthawa. Mtembowo utangokhudza mafupa a Elisa, munthuyo anakhalanso wamoyo+ ndipo anaimirira.+

22 Hazaeli+ mfumu ya Siriya inapondereza+ Aisiraeli masiku onse a Yehoahazi. 23 Koma Yehova anakomera mtima+ Aisiraeli ndi kuwachitira chifundo+ ndipo anatembenukira kwa iwo chifukwa cha pangano lake+ ndi Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Yakobo.+ Iye sanafune kuwawononga+ ndipo sanawachotse pamaso pake mpaka lero. 24 Pomaliza pake Hazaeli mfumu ya Siriya anamwalira, ndipo Beni-hadadi mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 25 Ndiyeno Yehoasi mwana wa Yehoahazi, analandanso kwa Beni-hadadi mwana wa Hazaeli, mizinda imene iye analanda Yehoahazi bambo ake pankhondo. Yehoasi anagonjetsa Beni-hadadi katatu, ndipo analandanso mizinda ya Isiraeli.+

14 M’chaka chachiwiri cha Yehoasi mwana wa Yehoahazi+ mfumu ya Isiraeli, Amaziya+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, anakhala mfumu. 2 Amaziya anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadini.+ 3 Iye anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova,+ koma osati ngati Davide kholo lake.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Yehoasi bambo ake anachita.+ 4 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+ 5 Ndiyeno ufumuwo utangokhazikika m’manja mwake, iye anayamba kupha+ atumiki ake amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+ 6 Koma ana a anthu akuphawo sanawaphe, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku la chilamulo cha Mose chimene Yehova analamula. Iye analamula kuti:+ “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo. Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+ 7 Amaziya anapha Aedomu+ okwana 10,000 m’chigwa cha Mchere+ n’kulanda mzinda wa Sela pankhondo. Kenako mzindawo anayamba kuutcha Yokiteeli ndipo dzina lake ndi lomweli mpaka lero.

8 Tsopano Amaziya anatumiza amithenga kwa Yehoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Isiraeli, ndi uthenga wakuti: “Bwera tidzamenyane.”+ 9 Yehoasi mfumu ya Isiraeli itamva inamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza+ wa ku Lebanoni, wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija.+ 10 Chifukwa chakuti iweyo wagonjetsa+ Edomu, mtima wako wayamba kudzikuza.+ Sangalala ndi ulemu umene wapeza+ ndipo khala m’nyumba mwako momwemo. N’chifukwa chiyani ukufuna kumenya nkhondo+ pamene zinthu sizikukuyendera bwino?+ Iweyo ndi Ayuda amene uli nawowo mugonja.” 11 Koma Amaziya sanamvere.+

Chotero Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anabwera, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anamenyana+ ku Beti-semesi+ m’dziko la Yuda. 12 Pankhondoyo, Ayuda anagonja pamaso pa Aisiraeli+ moti aliyense anathawira kuhema wake. 13 Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi mwana wa Ahaziya ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya n’kupita naye ku Yerusalemu, ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efuraimu+ mpaka kukafika pa Chipata cha Pakona.+ Anagumula mpata waukulu mikono 400.* 14 Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense, ndi ziwiya zonse zimene anazipeza panyumba ya Yehova+ ndi m’nyumba yosungiramo chuma cha mfumu. Anagwiranso anthu ena n’kubwerera ku Samariya.

15 Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zimene anachita, ndiponso zochita zake zamphamvu, komanso mmene anamenyanirana ndi Amaziya mfumu ya Yuda, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 16 Pomalizira pake, Yehoasi anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda ku Samariya+ pamodzi ndi mafumu a Isiraeli. Kenako Yerobowamu*+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

17 Amaziya+ mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, anakhalabe ndi moyo zaka 15+ pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli. 18 Nkhani zina zokhudza Amaziya zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.+ 19 Patapita nthawi, anthu ena anagwirizana zom’chitira chiwembu+ ku Yerusalemu, choncho iye anathawira ku Lakisi.+ Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko n’kukamuphera komweko.+ 20 Atatero anamunyamula pa mahatchi n’kukamuika m’manda+ ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ 21 Kenako anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya,*+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16,+ n’kumulonga ufumu m’malo mwa bambo ake Amaziya.+ 22 Mfumuyo itagona m’manda ndi makolo ake, Azariya anamanga mzinda wa Elati+ n’kuubwezera ku Yuda.

23 M’chaka cha 15 cha Amaziya mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Isiraeli anakhala mfumu ku Samariya, ndipo analamulira zaka 41. 24 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye machimo onse a Yerobowamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 25 Yerobowamu ndiye anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kunyanja ya Araba.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri amene anachokera ku Gati-heferi.+ 26 Yehova anali ataona mavuto aakulu omwe Aisiraeli anali kukumana nawo.+ Kunalibe ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake, ngakhalenso munthu aliyense woti akanathandiza Aisiraeli.+ 27 Yehova anali atalonjeza kuti sadzachotseratu dzina la Isiraeli padziko lapansi,+ choncho anawapulumutsa+ ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehoasi.

28 Nkhani zina zokhudza Yerobowamu ndi zonse zimene anachita, zochita zake zamphamvu ndiponso mmene anamenyera nkhondo, ndi mmene anabwezeretsera Damasiko+ ndi Hamati+ ku Yuda mu Isiraeli, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 29 Pomalizira pake, Yerobowamu anagona pamodzi ndi makolo ake, mafumu a Isiraeli, ndipo Zekariya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

15 M’chaka cha 27 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Azariya*+ mwana wa Amaziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 2 Azariya anayamba kulamulira ali ndi zaka 16, ndipo analamulira ku Yerusalemu+ zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu, ndipo dzina lawo linali Yekoliya. 3 Azariya anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Amaziya bambo ake anachita.+ 4 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+ 5 Pomaliza pake, Yehova anaichititsa khate mfumuyo+ moti inakhalabe yakhate+ mpaka tsiku limene inamwalira. Iyo inali kungokhala m’nyumba mwake osagwiranso ntchito.+ Pa nthawiyi, Yotamu+ mwana wa mfumuyo ndiye anali kuyang’anira nyumba ya mfumu ndi kuweruza+ anthu a m’dzikolo. 6 Nkhani zina zokhudza Azariya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 7 Pambuyo pake, Azariya anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Kenako Yotamu mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.+

8 M’chaka cha 38 cha Azariya+ mfumu ya Yuda, Zekariya+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa miyezi 6. 9 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova monga anachitira makolo ake.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 10 Ndiyeno Salumu mwana wa Yabesi anam’chitira chiwembu+ Zekariya n’kumupha+ ku Ibuleamu,+ ndipo iye anayamba kulamulira m’malo mwake. 11 Nkhani zina zokhudza Zekariya, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 12 Izi zinakwaniritsa mawu a Yehova+ amene anawalankhula kwa Yehu, akuti:+ “Ana+ ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.” Ndipo zinaterodi.+

13 Salumu mwana wa Yabesi, anakhala mfumu m’chaka cha 39 cha Uziya+ mfumu ya Yuda. Iye analamulira ku Samariya kwa mwezi umodzi wathunthu.+ 14 Ndiyeno Menahemu+ mwana wa Gadai, anachoka ku Tiriza+ kubwera ku Samariya n’kudzapha Salumu+ mwana wa Yabesi ku Samariyako. Kenako iye anayamba kulamulira m’malo mwake. 15 Nkhani zina zokhudza Salumu ndi chiwembu+ chimene anachita, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 16 Panali pa nthawi imeneyi pamene Menahemu anachoka ku Tiriza n’kupita kukaukira mzinda wa Tifisa, n’kupha anthu onse amene anali mmenemo. Anawononganso dera lozungulira mzindawo chifukwa anthu ake sanamutsegulire chipata, ndipo akazi onse apakati a mumzindawo anawatumbula.+

17 M’chaka cha 39+ cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadai anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 10. 18 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Masiku ake onse, sanasiye machimo onse a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 19 Tsopano Puli+ mfumu ya Asuri+ inabwera m’dzikomo. Choncho Menahemu anapatsa+ Puli matalente* 1,000 a siliva,+ kuti amuthandize kulimbitsa ufumu umene unali m’manja mwake.+ 20 Menahemu anatenga ndalama zasilivazo kwa Aisiraeli. Iye anatenga masekeli* 50 a siliva kwa mwamuna aliyense wachuma,+ ndipo anawapereka kwa mfumu ya Asuri. Pamenepo mfumu ya Asuri inabwerera ndipo sinakhale m’dzikomo. 21 Nkhani zina zokhudza Menahemu+ ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 22 Pomalizira pake Menahemu anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo Pekahiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

23 M’chaka cha 50 cha Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya+ kwa zaka ziwiri. 24 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 25 Kenako Peka+ mwana wa Remaliya, yemwe anali msilikali wake wom’thandiza pagaleta,+ anam’konzera chiwembu+ n’kumupha ku Samariya. Iye anapha mfumuyo ali limodzi ndi Arigobi ndi Ariye ndiponso amuna 50 a ku Giliyadi. Anaiphera munsanja yokhalamo ya panyumba ya mfumu,+ n’kuyamba kulamulira m’malo mwake. 26 Nkhani zina zokhudza Pekahiya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

27 M’chaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka+ mwana wa Remaliya+ anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 20. 28 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 29 M’masiku a Peka mfumu ya Isiraeli, Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri+ inabwera n’kulanda Iyoni,+ Abele-beti-maaka,+ Yanoa, Kedesi,+ Hazori,+ Giliyadi,+ ndi Galileya,+ dziko lonse la Nafitali.+ Inatenga anthu a m’madera amenewa n’kupita nawo ku Asuri.+ 30 Pamapeto pake, Hoshiya+ mwana wa Ela anakonzera chiwembu+ Peka mwana wa Remaliya n’kumupha.+ Kenako iye anayamba kulamulira m’malo mwake m’chaka cha 20 cha Yotamu+ mwana wa Uziya. 31 Nkhani zina zokhudza Peka ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

32 M’chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, Yotamu+ mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 33 Yotamu anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 34 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Uziya bambo ake anachita.+ 35 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo. Iye ndiye anamanga chipata chakumtunda cha nyumba ya Yehova.+ 36 Nkhani zina zokhudza Yotamu ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.+ 37 M’masiku amenewo Yehova anayamba kutumiza+ Rezini+ mfumu ya Siriya, ndi Peka+ mwana wa Remaliya kuti akalimbane ndi Yuda. 38 Pomalizira pake, Yotamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake. Kenako Ahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

16 M’chaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 2 Ahazi anali ndi zaka 20 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake monga anachitira Davide kholo lake.+ 3 Anayenda m’njira ya mafumu a ku Isiraeli,+ ndipo ngakhale mwana wake wamwamuna anamuwotcha* pamoto,+ mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa chifukwa cha ana a Isiraeli. 4 Ahazi ankafukiza ndi kupereka nsembe yautsi pamalo okwezeka,+ pamapiri,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+

5 Pa nthawi imeneyo Rezini+ mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anabwera kudzaukira Yerusalemu mwankhondo ndipo anazungulira Ahazi koma sanathe kumenyana naye.+ 6 Pa nthawiyo, Rezini mfumu ya Siriya anabwezeretsa mzinda wa Elati+ ku Edomu. Kenako anachotsa Ayuda mu Elati ndipo Aedomu analowa n’kumakhalamo. Iwo akukhalabe komweko mpaka lero. 7 Chotero Ahazi anatumiza amithenga kwa Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri ndi uthenga wakuti: “Ndine mtumiki wanu+ ndi mwana wanu. Bwerani mudzandipulumutse+ m’manja mwa mfumu ya Siriya ndi m’manja mwa mfumu ya Isiraeli, amene akundiukira.” 8 Pamenepo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anali panyumba ya Yehova+ ndiponso wochokera pa chuma cha m’nyumba ya mfumu, n’kuzitumiza kwa mfumu ya Asuri ngati chiphuphu.+ 9 Mfumu ya Asuri inamumvera n’kupita ku Damasiko+ ndipo inakalanda mzindawo.+ Anthu a mumzindawo inawatengera ku Kiri,+ ndipo Rezini+ inamupha.

10 Kenako Mfumu Ahazi+ inapita kukakumana ndi Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri ku Damasiko. Kumeneko inaonako guwa lansembe,+ chotero Mfumu Ahazi inatumizira wansembe Uliya chitsanzo cha kamangidwe ka guwa lansembe lonselo.+ 11 Wansembe Uliya+ anamanga guwa lansembelo.+ Analimanga mogwirizana ndi zonse zimene Mfumu Ahazi inam’tumizira kuchokera ku Damasiko, podikira kuti Mfumu Ahazi ibwereko ku Damasiko. 12 Mfumuyo itabwerako ku Damasiko, inaliona guwa lansembelo, ndipo inayamba kupita kuguwalo+ kukapereka nsembe.+ 13 Paguwa lansembelo, mfumuyo inapitiriza kuwotchapo+ nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu,+ ndi kuthirapo nsembe yachakumwa+ ndiponso kuwazapo magazi a nsembe zake zachiyanjano. 14 Tsopano guwa lansembe+ lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova, Ahazi analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo. Analichotsa pakati pa guwa lansembe latsopano ndi nyumba ya Yehova,+ n’kuliika kumpoto kwa guwa lake. 15 Ndiyeno Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uliya+ kuti: “Paguwa lansembe lalikululi uziwotchapo nsembe yopsereza yam’mawa,+ nsembe yambewu yamadzulo,+ nsembe yopsereza ya mfumu+ ndi nsembe yake yambewu, nsembe yopsereza ya anthu onse a m’dzikoli ndi nsembe yawo yambewu, ndiponso nsembe zawo zachakumwa. Magazi onse a nsembe yopsereza ndi magazi onse a nsembe zina uziwawaza paguwa langali. Koma guwa lansembe lamkuwalo, ndiona chochita nalo.” 16 Wansembe Uliya+ anachita mogwirizana ndi zonse zimene Mfumu Ahazi inalamula.+

17 Kuwonjezera apo, Mfumu Ahazi inaduladula+ malata a m’mbali+ mwa zotengera zokhala ndi mawilo,+ n’kuchotsa mabeseni+ pamwamba pa zotengerazo. Chosungiramo madzi+ inachichotsa pamwamba pa ng’ombe zamphongo zamkuwa+ n’kuchiika pansi pomanga ndi miyala. 18 Mfumuyo inachotsa chinthu chokhala ndi denga chogwiritsa ntchito pa sabata chimene anachimanga m’nyumba ya Yehova, ndipo inatsekanso khomo lakunja limene mfumu inali kulowera m’nyumbayo. Inachita zimenezi chifukwa choopa mfumu ya Asuri.

19 Nkhani zina zokhudza Ahazi ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 20 Pomalizira pake, Ahazi anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide+ pamodzi ndi makolo ake. Kenako Hezekiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

17 M’chaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoshiya+ mwana wa Ela anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya+ kwa zaka 9. 2 Hoshiya anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, koma osati ngati mmene anachitira mafumu a Isiraeli amene anakhalapo iye asanakhale.+ 3 Iye ndiye amene Salimanesere+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzamuthira nkhondo. Chotero Hoshiya anakhala mtumiki wake n’kuyamba kupereka msonkho+ kwa iye. 4 Koma mfumu ya Asuri inaona kuti Hoshiya anali kuichitira chiwembu,+ chifukwa chakuti iye anatumiza amithenga kwa So mfumu ya Iguputo,+ ndiponso sanapereke msonkho kwa mfumu ya Asuri monga anali kuchitira zaka zam’mbuyo. Choncho mfumu ya Asuri inam’manga n’kumutsekera m’ndende.+

5 Ndiyeno mfumu ya Asuri inabwera kudzachita nkhondo ndi dziko lonselo, kenako inazungulira mzinda wa Samariya+ kwa zaka zitatu. 6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+

7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ana a Isiraeli anachimwira+ Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa m’dziko la Iguputo+ n’kuwachotsa m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, ndipo anayamba kuopa milungu ina.+ 8 Iwo anapitiriza kuyenda motsatira malamulo+ a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, ndiponso motsatira malamulo amene mafumu a Isiraeli anapanga okha. 9 Ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo,+ ndipo anapitiriza kumanga malo okwezeka+ m’mizinda yawo yonse, kuyambira kunsanja+ ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. 10 Iwo anapitiriza kudziikira zipilala zopatulika+ ndi mizati yopatulika+ paphiri lililonse lalitali,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 11 Pamalo okwezeka onsewo, iwo anapitiriza kufukizapo nsembe yautsi, mofanana ndi mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa m’dzikolo chifukwa cha Aisiraeliwo. Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa zokwiyitsa+ Yehova.

12 Anapitiriza kutumikira mafano onyansa.*+ Ponena za mafano amenewa, Yehova anawauza kuti: “Musachite zimenezi.”+ 13 Yehova anali kuchenjeza+ Aisiraeli+ ndi Ayuda+ kudzera mwa aneneri ake onse+ ndi wamasomphenya aliyense,+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo sungani malamulo anga,+ mogwirizana ndi chilamulo chonse+ chimene ndinalamula makolo anu,+ ndi chimene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”+ 14 Koma iwo sanamvere. M’malomwake anaumitsa makosi awo,+ ngati mmene makolo awo anaumitsira makosi awo. Makolo awowo sanasonyeze chikhulupiriro+ mwa Yehova Mulungu wawo. 15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anapangana ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso+ zimene iye anali kuwachenjeza nazo. M’malomwake anayamba kutsatira mafano opanda pake+ ndipo iwowo nawonso anakhala opanda pake.+ Anatsatira mitundu imene inawazungulira, imene Yehova anawalamula kuti asamachite zofanana nayo.+

16 Anasiya malamulo onse+ a Yehova Mulungu wawo n’kudzipangira zifaniziro ziwiri za ana a ng’ombe,+ zopangidwa ndi zitsulo zosungunula,+ komanso mzati wopatulika.+ Anayamba kugwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kutumikira Baala.+ 17 Iwo anapitiriza kuwotcha* pamoto+ ana awo aamuna ndi aakazi, kulosera+ ndi kuwombeza.*+ Anapitirizanso+ kuchita zoipa* pamaso pa Yehova ndi cholinga chomukwiyitsa.+

18 Chotero Yehova anawakwiyira kwambiri+ Aisiraeli ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Sanasiye aliyense kupatulapo fuko la Yuda lokha.+

19 Komabe, nawonso Ayudawo sanasunge malamulo a Yehova Mulungu+ wawo, koma anayenda motsatira malamulo amene Aisiraeli+ anapanga. 20 Chotero Yehova anakana mbewu yonse+ ya Isiraeli ndipo anawasautsa n’kuwapereka m’manja mwa olanda katundu, mpaka iye anawathamangitsa pamaso pake.+ 21 Anang’amba Isiraeli kumuchotsa kunyumba ya Davide ndipo iwo analonga ufumu Yerobowamu mwana wa Nebati.+ Yerobowamuyo anasiyitsa Aisiraeli kutsatira Yehova n’kuwachimwitsa ndi tchimo lalikulu.+ 22 Ana a Isiraeli anapitiriza kuyenda m’machimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye, 23 mpaka Yehova anachotsa Isiraeli pamaso pake+ monga momwe ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Isiraeli anachoka m’dziko lake n’kupita ku Asuri, ndipo ali komweko mpaka lero.+

24 Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo,+ Kuta, Ava,+ Hamati,+ ndi Sefaravaimu+ n’kuwakhazika m’mizinda ya Samariya,+ m’malo mwa ana a Isiraeli. Anthuwo anatenga Samariya n’kumakhala m’mizinda yake. 25 Atayamba kukhala mmenemo, iwo sanaope+ Yehova. Choncho Yehova anatumiza mikango+ pakati pawo ndipo inapha ena a iwo. 26 Chotero mfumu ya Asuri inalandira uthenga wakuti: “Mitundu imene munaichotsa kwawo n’kukaikhazika m’mizinda ya ku Samariya, sikudziwa chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo, moti iye wakhala akutumiza mikango pakati pawo+ imene ikuwapha, popeza palibe amene akudziwa chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo.”

27 Pamenepo mfumu ya Asuri inalamula kuti: “Mutumize wansembe mmodzi+ mwa anthu amene munawagwira. Mumutumize kuchokera kumeneko, kuti apite kukakhala m’dzikolo n’kukaphunzitsa anthuwo chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo.” 28 Choncho mmodzi mwa ansembe amene anatengedwa kuchokera ku Samariya, anabwera n’kuyamba kukhala ku Beteli.+ Iye anakhala mphunzitsi pakati pawo wowaphunzitsa mmene angaopere Yehova.+

29 Koma mtundu uliwonse unapanga mulungu wake+ n’kukamuika m’kachisi m’malo okwezeka amene Asamariya anamanga. Mtundu uliwonse unachita zimenezi m’mizinda imene unali kukhala. 30 Anthu a ku Babulo anapanga Sukoti-benoti, a ku Kuta+ anapanga Nerigali, ndipo a ku Hamati anapanga Asima. 31 Aava+ anapanga Nibazi ndi Tarataka, pamene Asefaravaimu+ anali kuwotcha ana awo aamuna pamoto+ powapereka nsembe kwa Adarameleki ndi Anameleki, milungu ya Sefaravaimu. 32 Anthuwo ankaopa Yehova, koma anatenga anthu wamba a mitundu yawo n’kuwasandutsa ansembe+ a malo okwezeka, kuti aziwatumikira m’kachisi wa m’malo okwezeka. 33 Ankaopa Yehova+ koma ankalambira milungu yawo,+ mogwirizana ndi chipembedzo cha mitundu imene anawatengako.+

34 Mpaka lero akutsatirabe zipembedzo zawo zakale.+ Palibe amene ankaopa Yehova+ ndipo palibe amene ankatsatira malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi chilamulo+ chimene Yehova analamula ana a Yakobo.+ Yakoboyo Mulungu anamusintha dzina n’kumutcha Isiraeli,+ 35 pamene Yehova anachita nawo pangano+ n’kuwalamula kuti: “Musamaope milungu ina.+ Musamaigwadire kapena kuitumikira kapenanso kupereka nsembe kwa iyo.+ 36 Koma Yehova amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi mphamvu zazikulu, ndi dzanja lotambasula,+ ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene muyenera kumugwadira+ ndi kupereka nsembe kwa iye.+ 37 Muonetsetse kuti nthawi zonse mukutsatira+ malamulo,+ zigamulo,+ ndi chilamulo chimene anakulemberani,+ ndipo musamaope milungu ina. 38 Musaiwale pangano limene ndapangana nanu,+ ndipo musamaope milungu ina.+ 39 Koma muziopa Yehova+ Mulungu wanu, popeza iye ndi amene adzakupulumutseni m’manja mwa adani anu onse.”+

40 Koma iwo sanamvere. M’malomwake ankachita zinthu motsatira chipembedzo chawo chakale.+ 41 Mitundu imeneyi inali kuopa Yehova,+ koma inali kutumikira zifaniziro zawo zogoba. Mpaka lero, ana awo ndi zidzukulu zawo akuchitabe mmene makolo awo ankachitira.

18 M’chaka chachitatu cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Hezekiya+ mwana wa Ahazi,+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 2 Hezekiya anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abi mwana wa Zekariya.+ 3 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Davide kholo lake anachita.+ 4 Hezekiya ndiye anachotsa malo okwezeka,+ kugwetsa zipilala zopatulika,+ ndi kudula mzati wopatulika.+ Iye anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa+ imene Mose anapanga,+ chifukwa pofika masiku amenewo, ana a Isiraeli anakhala akufukiza nsembe+ yautsi kwa njoka yamkuwayo, ndipo inkatchedwa fano la njoka yamkuwa.+ 5 Iye anadalira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ Panalibenso mfumu ina yofanana naye pamafumu onse a Yuda+ amene anakhalapo iye asanakhale mfumu, ngakhalenso amene anakhalapo iye atafa.+ 6 Hezekiya anapitiriza kumamatira Yehova.+ Sanasiye kum’tsatira, koma anapitiriza kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose.+ 7 Yehova anakhala naye,+ ndipo kulikonse kumene ankapita anali kuchita zinthu mwanzeru.+ Anapandukira mfumu ya Asuri n’kukana kuitumikira.+ 8 Iye ndiye anapha Afilisiti+ mpaka ku Gaza+ ndi kumadera ake, kuyambira kunsanja ya alonda+ mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.

9 Tsopano m’chaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, kutanthauza chaka cha 7 cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Salimanesere+ mfumu ya Asuri anabwera ku Samariya n’kuzungulira mzindawo.+ 10 Pamapeto pa zaka zitatu, Asuriwo analanda mzindawo.+ Anaulanda m’chaka cha 6 cha Hezekiya, kutanthauza chaka cha 9 cha Hoshiya mfumu ya Isiraeli. Chotero Samariya analandidwa.+ 11 Pambuyo pake mfumu ya Asuri+ inatenga Aisiraeli n’kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala,+ ndi ku Habori+ pafupi ndi mtsinje wa Gozani, ndiponso m’mizinda ya Amedi.+ 12 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeliwo sanamvere+ mawu a Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake,+ ngakhalenso zonse zimene Mose+ mtumiki wa Yehova anawalamula.+ Iwo sanamvere kapena kuzichita.

13 M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo. 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Ndachimwa. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.”+ Chotero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente* 300 a siliva+ ndi matalente 30 a golide. 15 Ndiyeno Hezekiya anapereka siliva yense amene anali panyumba ya Yehova,+ ndiponso amene anali pa chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ 16 Pamenepo Hezekiya mfumu ya Yuda anachotsa zitseko za kachisi wa Yehova+ ndi mafelemu ake, zimene iye anazikuta+ ndi golide, n’kupereka golideyo kwa mfumu ya Asuri.

17 Kenako mfumu ya Asuri+ inatuma Tatani,*+ Rabisarisi,* ndi Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inawatumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iwo anapitadi n’kukaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 18 Kenako anayamba kuitana mfumu mofuula, ndipo kunabwera Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika.

19 Choncho Rabisake+ anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+ 20 Iwe wanena kuti (koma ndi mawu a pakamwa chabe), ‘Ine ndili ndi nzeru+ ndi mphamvu zofunika pankhondo.’ Kodi ukudalira ndani popandukira+ ine? 21 Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika+ loti munthu ataligwira kuti limuchirikize, lingamucheke m’manja. Umu ndi mmene Farao+ mfumu ya Iguputo alili kwa onse omudalira. 22 Ngati amuna inu mungandiuze kuti, ‘Tikudalira+ Yehova Mulungu wathu,’+ kodi si iye amene Hezekiya+ wam’chotsera malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe, n’kuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada patsogolo pa guwa lansembe ili, la ku Yerusalemu’?”’+ 23 Tsopano ubetcherane+ ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti ndione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.+ 24 Kodi ungathe bwanji kubweza bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga,+ pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta+ ndi okwera pamahatchi?+ 25 Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza+ kuti, ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo, ndipo ukaliwononge.’”

26 Pamenepo Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya, Sebina,+ ndi Yowa+ anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu m’chilankhulo cha Asiriya+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.” 27 Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene mawuwa kwa mbuye wanu yekha ndi kwa inuyo? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, kuti adye chimbudzi chawo+ ndi kumwa mkodzo wawo limodzi nanu?”+

28 Choncho Rabisake akadali chiimire, anapitiriza kulankhula mokweza m’chilankhulo cha Ayuda,+ ndipo anati: “Imvani mawu a mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri. 29 Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni anthu inu, chifukwa sangathe kukulanditsani m’manja mwanga.+ 30 Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Mosakayikira Yehova atilanditsa,+ ndipo mzindawu superekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 31 Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Ndigonjereni, ndipo bwerani kwa ine. Aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu,+ komanso aliyense azimwa madzi a m’chitsime chake,+ 32 kufikira ine nditabwera kudzakutengerani kudziko lofanana ndi dziko lanulo+ kuti mukhalebe ndi moyo osafa. Ndidzakutengerani kudziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate+ ndi minda ya mpesa,+ dziko la mitengo ya maolivi a mafuta ndiponso la uchi.+ Musamvere Hezekiya chifukwa akukunyengererani ndi mawu akuti, ‘Yehova atilanditsa.’+ 33 Kodi pali mulungu wa mitundu ina amene wakwanitsa kupulumutsa+ mtundu wake m’manja mwa mfumu ya Asuri?+ 34 Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu,+ Hena,+ ndi Iva?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+ 35 Ndi mulungu uti pakati pa milungu yonse ya mayiko, amene walanditsa dziko lake m’manja mwanga,+ kuti Yehova athe kulanditsa Yerusalemu m’manja mwanga?”’”+

36 Anthuwo anangokhala chete+ osamuyankha,+ chifukwa lamulo lochokera kwa mfumu linali lakuti: “Musamuyankhe.”+ 37 Koma Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atang’amba zovala zawo+ n’kumuuza mawu a Rabisake.

19 Mfumu Hezekiya+ itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake+ n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+ 2 Komanso, inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina+ mlembi, ndi akuluakulu a ansembe, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula,+ tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka,+ koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu amva+ mawu onse a Rabisake, amene mbuye wake mfumu ya Asuri yam’tuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira+ amene alipo.’”

5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.+ 7 Ndiika maganizo mwa iye,+ kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+

8 Koma Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Mfumuyo inamva kuti Tirihaka mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Choncho inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10 “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukum’dalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu+ saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse amene anawawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12 Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa? Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara?+ 13 Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena, ndi Iva?’”+

14 Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova n’kukaitambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera+ pamaso pa Yehova, kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi,+ inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse+ a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba+ ndi dziko lapansi.+ 16 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu a Senakeribu amene watumiza kudzatonza nawo+ Mulungu wamoyo. 17 N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mitundu ndi mayiko awo.+ 18 Atentha milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga. 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+

20 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya, wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Ndamva pemphero+ limene wapemphera kwa ine lokhudza Senakeribu mfumu ya Asuri.+ 21 Awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:

“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza+ ndipo wakuseka.+

Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu+ wakupukusira mutu.+

22 Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+

Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+

Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+

Ndi Woyera wa Isiraeli!+

23 Kudzera mwa amithenga ako+ watonza Yehova ndipo wanena kuti,+

‘Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+

Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+

Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+

Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza+ italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+

Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+

24 Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi achilendo,

Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+

25 Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale, izi n’zimene ndidzachite.+

Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+

Tsopano ndizichita.+

Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+

26 Anthu okhala m’mizindayo adzafooka manja.+

Adzachita mantha kwambiri ndiponso adzachita manyazi.+

Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+

Ngati udzu womera padenga+ ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+

27 Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+

Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+

28 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga,+

Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+

Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+

29 “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:+ Chaka chino mudya mmera wa mbewu zimene zinagwera pansi.+ M’chaka chachiwiri mudzadya mbewu zongomera zokha, koma m’chaka chachitatu, anthu inu mudzabzale mbewu+ n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa ndi kudya zipatso zake.+ 30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 31 Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+

32 “‘N’chifukwa chake Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi,+ kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo* pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.+ 33 Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno, ndiwo mawu a Yehova.+ 34 Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+

35 Ndiyeno usiku umenewo, mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri+ n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 36 Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri inachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Ninive.+ 37 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

20 M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+ 2 Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova+ kuti: 3 “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+

4 Pamene Yesaya anali kutuluka, asanafike n’komwe pabwalo lapakati, mawu a Yehova anam’fikira,+ akuti: 5 “Bwerera, kauze Hezekiya mtsogoleri+ wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu+ wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva+ pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+ 6 Ndithu ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako, ndipo ndidzalanditsa+ iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri. Ndidzateteza mzinda uno chifukwa cha ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+

7 Kenako Yesaya anati: “Amuna inu, tengani nkhuyu zouma zoumba pamodzi.”+ Choncho iwo anatenga nkhuyuzo n’kuziika pachithupsa+ chimene anali nacho, ndipo Hezekiya anachira pang’onopang’ono.+

8 Pa nthawiyi, Hezekiya anafunsa Yesaya kuti: “Kodi chizindikiro chakuti Yehova andichiritsa, ndi kuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu n’chiyani?”+ 9 Yesaya anayankha kuti: “Chizindikiro+ chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi: Kodi mthunzi uyende masitepe 10 kupita kutsogolo, kapena uyende masitepe 10 kubwerera m’mbuyo pamasitepe olowera m’nyumba?” 10 Hezekiya anayankha kuti: “N’zosavuta kuti mthunzi upite kutsogolo masitepe 10, koma osati kubwerera m’mbuyo masitepe 10.”+ 11 Pamenepo mneneri Yesaya anayamba kufuulira Yehova, ndipo iye anachititsa mthunzi umene unali utapita kale kutsogolo kuti ubwerere m’mbuyo pang’onopang’ono pamasitepe a Ahazi. Mthunziwo unabwerera m’mbuyo masitepe 10.+

12 Pa nthawi imeneyo, Berodaki-baladani+ mwana wa Baladani mfumu ya Babulo,+ anatumiza makalata+ ndi mphatso kwa Hezekiya chifukwa anamva kuti Hezekiya anali kudwala. 13 Hezekiya anawamvetsera anthuwo ndipo anawaonetsa zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide,+ mafuta a basamu,+ mafuta abwino, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo, ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake ndi mu ufumu wake wonse.+

14 Pambuyo pake mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya n’kuifunsa kuti:+ “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, ndipo anachokera kuti?”+ Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.” 15 Ndiyeno Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani m’nyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili m’nyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”+

16 Tsopano Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imvani mawu a Yehova.+ 17 ‘“Masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili m’nyumba mwako,+ ndi zonse zimene makolo ako akhala akusunga kufikira lero, anthu adzazitenga n’kupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,”+ watero Yehova. 18 “Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna+ za panyumba ya mfumu ya ku Babulo.”’”+

19 Pamenepo Hezekiya anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwalankhulawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Ngati mtendere ndi chilungamo+ zipitirire m’masiku anga, ndiye kuti zili bwino, si choncho?”+

20 Nkhani zina zokhudza Hezekiya ndi zochita zake zonse zamphamvu, ndiponso mmene anakumbira dziwe+ ndi ngalande+ n’kubweretsa madzi mumzindawo, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 21 Pomalizira pake, Hezekiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Manase+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

21 Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Hefiziba. 2 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa za mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli. 3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Baala n’kumanga mzati wopatulika, monga momwe Ahabu+ mfumu ya Isiraeli anachitira. Iye anayambanso kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+ 4 Anamanga maguwa ansembe m’nyumba ya Yehova,+ imene ponena za iyo Yehova anati: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+ 5 Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* mwana wake wamwamuna pamoto,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,*+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu ndi olosera+ zam’tsogolo. Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.

7 Komanso iye anaika m’nyumbayo chifaniziro+ cha mzati wopatulika chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo,+ Yehova anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+ 8 Sindidzachititsanso phazi la Isiraeli kuchoka panthaka imene ndinapatsa makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anawalamula.” 9 Koma sanamvere,+ ndipo Manase anapitiriza kunyengerera anthu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu+ yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.

10 Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri,+ kuti: 11 “Manase+ mfumu ya Yuda yachita zinthu zonyansazi.+ Yachita zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene anachita Aamori+ amene analiko iye asanakhale mfumu. Iye wachimwitsa ngakhale Yuda+ ndi mafano ake onyansa. 12 Pa chifukwa chimenechi Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikubweretsa tsoka pa Yerusalemu+ ndi Yuda loti aliyense akamva, adzadabwa kwambiri.*+ 13 Ndithu ndidzayeza Yerusalemu ndi chingwe chimene ndinayezera+ Samariya,+ ndiponso ndidzamuyeza ndi thabwa lowongolera limene ndinayezera nyumba ya Ahabu.+ Yerusalemu ndidzam’pukuta+ mpaka kuyera mbee ngati mmene munthu amapukutira mbale yolowa mpaka kuyera mbee, n’kuitembenuza.+ 14 Ndidzataya otsala+ a cholowa changa+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo. Iwo adzakhala zofunkha ndipo katundu wawo adzalandidwa ndi adani awo onse.+ 15 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti iwo anachita zoipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuyambira tsiku limene makolo awo anatuluka ku Iguputo mpaka lero.’”+

16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 17 Nkhani zina zokhudza Manase ndi zonse zimene anachita, ndiponso tchimo lake limene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 18 Pomalizira pake, Manase anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda m’munda wa panyumba pake, m’munda wa Uziza.+ Kenako Amoni mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

19 Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri+ ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Yotiba, ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20 Amoni anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase bambo ake.+ 21 Iye anapitiriza kuyenda m’njira zonse zimene bambo ake anayendamo,+ ndipo anapitiriza kutumikira mafano onyansa+ amene bambo ake anawatumikira, n’kumawagwadira. 22 Chotero anasiya Yehova,+ Mulungu wa makolo ake, ndipo sanayende m’njira ya Yehova.+ 23 Pomaliza pake, atumiki a mfumu Amoni anam’chitira chiwembu n’kumupha+ m’nyumba mwake momwe. 24 Koma anthu a m’dzikolo anapha anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni. Kenako anthu a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake. 25 Nkhani zina zokhudza Amoni ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 26 Chotero anamuika m’manda ake m’munda wa Uziza,+ ndipo Yosiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

22 Yosiya+ anali ndi zaka 8 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya. 2 Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda m’njira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.+

3 M’chaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, mfumuyo inatuma Safani+ mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu yemwe anali mlembi, kuti apite kunyumba ya Yehova. Inam’tuma ndi mawu akuti: 4 “Pita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe,+ ukamuuze kuti asonkhanitse pamodzi ndalama zonse+ zimene zikubwera kunyumba ya Yehova,+ zimene alonda a pakhomo+ atolera kwa anthu. 5 Azipereke kwa ogwira ntchito+ osankhidwa a m’nyumba ya Yehova, kuti akazipereke kwa amene akugwira ntchitoyo m’nyumba ya Yehova, kuti amate ming’alu ya nyumbayo.+ 6 Aziperekenso kwa amisiri, kwa omanga nyumba, ndi kwa amisiri omanga ndi miyala, komanso agulire matabwa ndi miyala yosema kuti akonzere nyumbayo.+ 7 Koma anthu amene akupatsidwa ndalamawo asafunsidwe mmene ayendetsera ndalamazo,+ chifukwa akugwira ntchito mokhulupirika.”+

8 Kenako Hilikiya+ mkulu wa ansembe anauza Safani+ mlembi+ kuti: “Ndapeza buku la chilamulo+ m’nyumba ya Yehova!” Choncho Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani, ndipo iye anayamba kuliwerenga. 9 Tsopano Safani mlembi anapita kwa mfumu n’kuiuza kuti: “Atumiki anu akhuthula ndalama zimene anazipeza m’nyumbayo, ndipo akuzipereka kwa ogwira ntchito osankhidwa a m’nyumba ya Yehova.”+ 10 Kenako Safani mlembi anauza mfumuyo kuti: “Pali buku+ limene wansembe Hilikiya wandipatsa.” Ndiyeno Safani anayamba kuwerenga bukulo pamaso pa mfumu.

11 Mfumuyo itangomva mawu a m’buku la chilamulolo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.+ 12 Kenako mfumuyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi, ndi Asaya+ mtumiki wa mfumu, kuti: 13 “Pitani mukafunse+ kwa Yehova m’malo mwa ineyo, m’malo mwa anthuwa, ndi m’malo mwa Yuda yense. Mukafunse zokhudza mawu a m’buku limene lapezekali, chifukwa mkwiyo wa Yehova+ umene watiyakira ndi waukulu, popeza makolo+ athu sanamvere mawu a m’buku ili. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”+

14 Chotero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani, ndi Asaya anapita kukalankhula ndi Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe anali wosamalira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi,+ ndipo Hulidayo anali kukhala kumbali yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 15 Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Amuna inu, kauzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti: 16 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka+ pamalo ano ndi anthu ake,+ kukwaniritsa mawu onse+ a m’buku limene mfumu ya Yuda yawerenga,+ 17 chifukwa chakuti andisiya n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho mkwiyo wanga wayakira malo ano ndipo suzimitsidwa.’”’+ 18 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ponena za mawu amene wamvawo,+ 19 chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Yehova utamva zimene ndanena zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chodabwitsa ndi temberero,+ unang’amba+ zovala zako n’kuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva,” ndiwo mawu a Yehova.+ 20 “N’chifukwa chake ndidzakugoneka+ pamodzi ndi makolo ako, ndipo ndithu udzaikidwa m’manda ako mu mtendere.+ Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndikulibweretsa pamalo ano.”’” Choncho iwo anabweretsa mawuwo kwa mfumuyo.

23 Kenako mfumuyo inatumiza uthenga kwa akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasonkhana kwa mfumuyo.+ 2 Ndiyeno mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova pamodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu onse okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ aneneri, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu.+ Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku+ la pangano+ limene linapezeka m’nyumba ya Yehova.+ 3 Mfumuyo inaimirira pafupi ndi chipilala+ ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti adzatsatira+ Yehova ndi kusunga malamulo ake+ ndi maumboni* ake.+ Adzachita zimenezi ndi mtima wonse+ ndi moyo wonse,+ mwa kutsatira mawu a pangano olembedwa m’bukulo.+ Choncho anthu onsewo anavomereza panganolo.+

4 Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ansembe ena, ndi alonda a pakhomo+ kuti atulutse m’kachisi wa Yehova ziwiya zonse zimene anapangira Baala,+ mzati wopatulika,+ ndi khamu lonse la zinthu zakuthambo.+ Itatero, inakazitentha kunja kwa Yerusalemu pamalo otsetsereka a ku Kidironi,+ ndipo inabweretsa phulusa lake ku Beteli.+ 5 Mfumuyo inachotsa ntchito ansembe a milungu yachilendo, amene mafumu a Yuda anawaika kuti azifukiza nsembe yautsi pamalo okwezeka m’mizinda ya Yuda ndi malo ozungulira Yerusalemu. Inachotsanso ntchito ansembe ofukiza nsembe yautsi kwa Baala,+ kwa dzuwa, kwa mwezi, kwa magulu a nyenyezi, ndi kwa khamu lonse la zinthu zakuthambo.+ 6 Kuwonjezera apo, mfumuyo inatulutsa mzati wopatulika+ umene unali m’nyumba ya Yehova, ndipo inapita nawo kuchigwa* cha Kidironi kunja kwa mzinda wa Yerusalemu n’kukautentha+ kuchigwacho. Itatero, inauperapera n’kuwaza fumbi lake pamanda+ a ana a anthu. 7 Inagwetsanso nyumba za mahule achimuna a pakachisi+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, mmene akazi anali kulukiramo akachisi a mahema a mzati wopatulika.

8 Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera m’mizinda ya Yuda. Inawaitanitsa kuti isandutse malo okwezeka kukhala osayenera kulambirako, kumene ansembewo ankafukizako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba.+ Inagwetsa malo okwezeka a pazipata amene anali pakhomo la pachipata cha Yoswa mkulu wa mzindawo. Chipata cha Yoswacho chinali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pachipata cha mzindawo. 9 Koma ansembe+ a malo okwezekawo sankabwera kuguwa lansembe la Yehova ku Yerusalemu. M’malomwake, ankadya mikate yopanda chofufumitsa+ pakati pa abale awo. 10 Mfumuyo inachititsa kuti ku Tofeti,+ m’chigwa cha ana a Hinomu+ kukhale kosayenera kulambirako, kuti munthu aliyense asawotcheko* mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi pamoto,+ pomupereka kwa Moleki.+ 11 Komanso inachititsa kuti mahatchi amene mafumu a Yuda anawapereka kwa dzuwa, asiye kulowa m’nyumba ya Yehova kudzera m’chipinda chodyera+ cha Natani-meleki, nduna ya panyumba ya mfumu, chimene chinali pakhonde. Nawonso magaleta a dzuwa+ inawatentha pamoto. 12 Kenako mfumuyo inagumula maguwa ansembe amene anali padenga la chipinda chapadenga+ cha Ahazi, amene mafumu a Yuda anamanga. Inagumulanso maguwa ansembe+ amene Manase anamanga pamabwalo awiri a nyumba ya Yehova. Itatero, inawaperapera komweko ndipo fumbi lake inakaliwaza kuchigwa* cha Kidironi. 13 Malo okwezeka amene anali kutsogolo+ kwa Yerusalemu kudzanja lamanja* la Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo+ mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti+ chonyansa cha Asidoni, Kemosi+ chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu+ chonyansa cha ana a Amoni, mfumuyo inawasandutsa osayenera kulambirako. 14 Inaphwanyaphwanya+ zipilala zopatulika ndipo inagwetsanso mizati yopatulika. Pamalo pamene panali zimenezi inadzazapo mafupa a anthu. 15 Komanso guwa lansembe limene linali ku Beteli+ ndi malo okwezeka amene Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa Isiraeli+ anamanga, ngakhale guwa lansembe limenelo ndi malo okwezekawo, mfumuyo inagumula. Kenako inatentha malo okwezekawo n’kuwaperapera mpaka kusanduka fumbi. Inatenthanso mzati wopatulika.

16 Yosiya atatembenuka, anaona manda amene anali m’phirimo. Choncho anatumiza anthu kuti akatenge mafupa m’mandawo, ndipo anawatentha+ paguwa lansembelo kuti alisandutse losayenera kulambirapo, mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene munthu wa Mulungu woona uja, amene analengeza+ zinthu zimenezi, ananena. 17 Kenako iye anati: “Kodi chipilala chimene ndikuchiona apocho n’cha chiyani?” Pamenepo amuna a mumzindawo anamuyankha kuti: “Ndi manda+ a munthu wa Mulungu woona amene anachokera ku Yuda,+ n’kulengeza zinthu zotsutsa guwa lansembe la ku Beteli, zimene mwachita inuzi.”+ 18 Choncho iye anati: “Musiyeni apume.+ Musalole aliyense kudodometsa mafupa ake.” Chotero iwo sanakhudze mafupa akewo limodzi ndi mafupa a mneneri+ amene anachokera ku Samariya.

19 Yosiya anachotsanso akachisi onse+ a m’malo okwezeka amene anali m’mizinda+ ya ku Samariya, amene mafumu+ a Isiraeli anamanga kuti akwiyitse Mulungu.+ Iye anawachitira zofanana ndi zonse zimene anachita ku Beteli.+ 20 Chotero iye anapha ansembe onse+ a m’malo okwezeka n’kuwapereka nsembe pamaguwa ansembe kumeneko. Kenako anawotcha mafupa a anthu pamaguwa ansembewo.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

21 Tsopano mfumuyo inalamula anthu onse kuti: “Chitirani pasika+ Yehova Mulungu wanu, malinga ndi zimene zalembedwa m’buku la panganoli.”+ 22 Pakuti pasika ngati ameneyu anali asanachitikepo kuyambira masiku a oweruza amene anaweruza Isiraeli,+ ngakhalenso masiku onse a mafumu a Isiraeli ndi mafumu a Yuda.+ 23 Koma m’chaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, iwo anachitira Yehova pasika ameneyu ku Yerusalemu.+

24 Yosiya anachotsanso anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera+ zam’tsogolo. Anachotsanso aterafi,*+ mafano onyansa,+ ndi zonyansa+ zonse zimene zinali m’dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu, kuti atsatire mawu a chilamulo+ amene analembedwa m’buku+ limene wansembe Hilikiya analipeza panyumba ya Yehova.+ 25 Panalibenso mfumu ina iye asanakhale mfumu imene inabwerera+ kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse,+ ndi mphamvu zake zonse, mogwirizana ndi chilamulo chonse cha Mose. Ngakhale pambuyo pake sipanakhalenso mfumu ina ngati iyeyo.

26 Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene unayakira Yuda,+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anawachititsa, n’kukwiyitsa nazo Mulungu.+ 27 Koma Yehova anati: “Yuda+ nayenso ndim’chotsa pamaso panga+ monga mmene ndinachotsera Isiraeli,+ ndipo ndithu ndidzakana ngakhale mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala pamenepo.’”+

28 Nkhani zina zokhudza Yosiya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 29 M’masiku ake, Farao Neko+ mfumu ya Iguputo inabwera kudzathandiza mfumu ya Asuri pamtsinje wa Firate,+ ndipo Mfumu Yosiya inapita kukamenyana ndi mfumu ya Iguputoyo,+ koma mfumuyo inapha Yosiya+ ku Megido+ itangomuona. 30 Choncho atumiki ake ananyamula mtembo wake pagaleta kuchokera ku Megido n’kupita nawo ku Yerusalemu+ kumene anakauika m’manda ake. Kenako anthu a m’dzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya n’kumudzoza ndi kumulonga ufumu m’malo mwa bambo ake.

31 Yehoahazi anali ndi zaka 23+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina, ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 32 Iye anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake akale anachita.+ 33 Kenako Farao Neko+ anamanga+ Yehoahazi ku Ribila+ m’dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Ndiyeno Farao Neko analamula+ dzikolo kuti lim’patse matalente 100 a siliva+ ndi talente imodzi ya golide.+ 34 Kuwonjezera apo, Farao Neko anaika Eliyakimu+ mwana wa Yosiya kukhala mfumu m’malo mwa Yosiya bambo ake, n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Atatero anatenga Yehoahazi n’kupita naye ku Iguputo, kumene anakafa pamapeto pake.+ 35 Yehoyakimu anapereka siliva+ ndi golide kwa Farao. Koma ankakhometsa msonkho+ anthu a m’dzikolo kuti apereke silivayo kwa Farao, monga mmene anamulamulira. Iye anatenga siliva ndi golide kwa anthuwo kuti apereke kwa Farao Neko, malinga ndi msonkho umene munthu aliyense+ ankayenera kupereka.

36 Yehoyakimu anali ndi zaka 25+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Ruma, ndipo dzina lawo linali Zebida mwana wa Pedaya. 37 Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake anachita.+

24 M’masiku ake, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzachita nkhondo ndi Yerusalemu. Choncho Yehoyakimu anakhala mtumiki wake+ kwa zaka zitatu, koma kenako anam’pandukira. 2 Tsopano Yehova anayamba kum’tumizira Yehoyakimu magulu a achifwamba a Akasidi,+ a Asiriya, a Amowabu,+ ndi a ana a Amoni. Ankawatumiza ku Yuda kuti awononge dzikolo mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri. 3 Zimenezi zinachitikira Yuda molamulidwa ndi Yehova, kuti achotse+ dzikolo pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase,+ malinga ndi zonse zimene anachita, 4 komanso chifukwa cha magazi osalakwa+ amene iye anakhetsa, moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa, ndipo Yehova sanalole kukhululuka.+

5 Nkhani zina zokhudza Yehoyakimu+ ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 6 Pomalizira pake Yehoyakimu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Yehoyakini mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

7 Mfumu ya Iguputo sinatulukenso+ m’dziko lake,+ chifukwa mfumu ya Babulo inali itatenga zinthu zonse zomwe zinali za mfumu ya Iguputo,+ kuyambira kuchigwa*+ cha Iguputo kukafika kumtsinje wa Firate.+

8 Yehoyakini+ anali ndi zaka 18 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Nehusita mwana wa Elinatani. 9 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene bambo ake anachita.+ 10 Pa nthawi imeneyo, atumiki a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu n’kuzungulira mzindawo.+ 11 Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo atumiki ake atauzungulira.+

12 Patapita nthawi, Yehoyakini mfumu ya Yuda anatuluka n’kupita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake,+ atumiki ake, akalonga ake, ndi nduna za panyumba yake, ndipo mfumu ya Babuloyo inam’tengera Yehoyakini ku ukapolo m’chaka cha 8+ cha ufumu wake. 13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera. 14 Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo. 15 Chotero iye anatengera Yehoyakini+ ku Babulo.+ Anatenga ku Yerusalemu mayi a mfumuyo,+ akazi ake, nduna za panyumba yake,+ ndi akuluakulu a m’dzikolo, n’kuwapititsa ku Babulo. 16 Mfumu ya Babulo inatengera ku Babulo amuna onse olimba mtima okwana 7,000, amisiri ndi anthu omanga makoma achitetezo okwana 1,000, ndi amuna onse amphamvu omenya nkhondo.+ 17 Komanso mfumu ya Babulo+ inatenga Mataniya, bambo ake aang’ono+ a Yehoyakini, n’kuwaika kukhala mfumu m’malo mwake. Kenako inam’sintha dzina Mataniya kuti akhale Zedekiya.+

18 Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina, ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 19 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+ 20 Zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda zinakwiyitsa+ kwambiri Yehova ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.+

25 M’chaka cha 9+ cha ufumu wa Zedekiya, m’mwezi wa 10,+ pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ ku Yerusalemu pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo. Anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo ndipo anamanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+ 2 Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya. 3 M’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,+ njala+ inafika poipa kwambiri mumzindawo, ndipo anthu a m’dzikolo analibiretu chakudya.+ 4 Ndiyeno khoma la mzindawo linabooledwa,+ ndipo amuna onse ankhondo anathawa usiku kudzera pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu.+ Akasidi+ anali atazungulira mzinda wonsewo, ndipo mfumuyo inayamba kuthawa+ kulowera cha ku Araba.+ 5 Gulu lankhondo la Akasidi+ linayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo linaipeza+ m’chipululu cha Yeriko.+ Pamenepo gulu lonse lankhondo la mfumuyo linabalalika n’kuisiya yokha. 6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ n’kupita nayo ku Ribila+ kwa mfumu ya Babulo, kuti akaiuze chigamulo chake. 7 Iwo anapha ana a Zedekiya iye akuona,+ kenako Zedekiyayo anam’chititsa khungu.+ Atatero anamumanga ndi maunyolo amkuwa+ n’kupita naye ku Babulo.+

8 M’mwezi wachisanu, pa tsiku la 7 la mweziwo, kutanthauza m’chaka cha 19+ cha Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+ 9 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba zonse za mu Yerusalemu,+ ndi nyumba ya munthu aliyense wotchuka.+ 10 Kenako gulu lonse lankhondo la Akasidi, lomwe linali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, linagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+ 11 Anthu ena onse amene anatsala mumzindamo, ndi anthu amene anapita kumbali ya mfumu ya Babulo, ndiponso anthu ena onse,+ Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+ 12 Ena mwa anthu onyozeka+ a m’dzikolo, mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi alimi ogwira ntchito mokakamizidwa.+ 13 Zipilala+ zamkuwa zimene zinali m’nyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wake kupita nawo ku Babulo.+ 14 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu, ndi ziwiya zonse+ zamkuwa zimene ansembe anali kugwiritsira ntchito potumikira. 15 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa zomwe zinali zagolide weniweni,+ komanso zomwe zinali zasiliva weniweni.+ 16 Koma panalibe njira yodziwira kulemera kwa mkuwa wa zipilala ziwiri zija, chosungiramo madzi chimodzi chija, ndi zotengera zokhala ndi mawilo zimene Solomo anapangira nyumba ya Yehova. Panalibe njira yodziwira kulemera kwa mkuwa wa ziwiya zonsezi.+ 17 Chipilala chilichonse kutalika kwake chinali mikono 18,+ ndipo mutu+ wake unali wamkuwa. Mutuwo kutalika kwake kunali mikono itatu, ndipo maukonde ndi makangaza*+ amene anazungulira mutuwo, onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa.

18 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri, ndi alonda atatu a pakhomo.+ 19 Mumzindawo anatengamo nduna imodzi ya panyumba ya mfumu imene inali kuyang’anira amuna ankhondo. Anatenganso amuna asanu kuchokera pa anthu amene ankatha kuonana ndi mfumu mwa amuna amene anali mumzindamo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe anali kusonkhanitsa ankhondo a m’dzikolo, ndi amuna 60 mwa anthu a m’dzikolo amene anali mumzindawo.+ 20 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa+ n’kupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 21 Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo+ ku Ribila m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+

22 Ndiyeno Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anasankha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani,+ kuti akhale mtsogoleri wa anthu+ amene anatsala m’dziko la Yuda, amene mfumuyo inawasiya mmenemo. 23 Akuluakulu onse a magulu ankhondo+ ndi asilikali awo atamva kuti mfumu ya Babulo yasankha Gedaliya, nthawi yomweyo anapita kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Akuluakuluwo anali Isimaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti Mnetofa, ndi Yaazaniya mwana wa Amaakati, pamodzi ndi asilikali awo. 24 Gedaliya analumbirira+ akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kukhala atumiki a Akasidi. Khalani m’dzikoli n’kumatumikira mfumu ya Babulo, ndipo zinthu zikuyenderani bwino.”+

25 Tsopano m’mwezi wa 7,+ Isimaeli+ mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, anapita kwa Gedaliya pamodzi ndi amuna 10. Isimaeli anali wa m’banja lachifumu. Iye pamodzi ndi amunawo anapha Gedaliya+ ndi Ayuda ndiponso Akasidi amene anali naye pamodzi ku Mizipa.+ 26 Zitatero, anthu onse, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu ndi akuluakulu a magulu ankhondo, ananyamuka n’kupita ku Iguputo,+ chifukwa anayamba kuopa Akasidi.+

27 M’chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 12, pa tsiku la 27 la mweziwo, chaka chimene Evili-merodaki+ mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima+ Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende. 28 Kenako anayamba kulankhula naye zinthu zabwino, ndipo anakweza* ufumu wake kuposa mafumu ena amene anali naye limodzi ku Babulo.+ 29 Yehoyakini anavula zovala zake za kundende,+ ndipo nthawi zonse anali kudya chakudya+ pamaso pa mfumuyo masiku onse a moyo wake. 30 Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya+ kuchokera kwa mfumuyo, masiku onse a moyo wake.

Ameneyu anali m’bale wake wa Ahaziya.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kapena kuti “kapatsindwi.”

Ena amati, “chipupa” kapena “chikupa.”

Kapena “balere.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Zitosi za nkhunda zodzaza manja awiri zinali zokwana pafupifupi gawo limodzi la magawo atatu a lita.

Ena amati “saka.”

Onani Zakumapeto 12.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

“Rama” ndi chidule cha Ramoti-giliyadi.

Mawu ake enieni, “Kokera chovala chako m’chiuno n’kuchimanga.”

Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.

Mawu ake enieni, “Kudzera kunyumba ya kumunda.”

Mawu ake enieni, “Yeretsani.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “Phewa lakumanja,” kutanthauza mbali ya kum’mwera, munthu akayang’ana kum’mawa.

Mawu ake enieni, “Phewa lakumanzere,” kutanthauza mbali ya kumpoto, munthu akayang’ana kum’mawa.

Mawu ake enieni, “Anatembenuza nkhope yake kuti apite.”

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.

Uyu ndi Yerobowamu Wachiwiri.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Uyu ndi Yerobowamu Wachiwiri.

Azariya amatchedwanso Uziya.

Azariya amatchedwanso Uziya.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Mawu ake enieni, “Anamudutsitsa pamoto.”

Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Mawu ake enieni, “Kudutsitsa pamoto.”

Mawu akuti “kuwombeza” akutanthauza kufuna kudziwa zam’tsogolo, kapena kufufuza ngati zochitika kapena zinthu zinazake zikulosera kuti m’tsogolo mudzachitika zabwino kapena zoipa.

Kapena kuti “anatsimikiza mtima kuti achite zinthu zoipa.”

Onani Zakumapeto 12.

Kapena kuti “mkulu wa asilikali.”

Kapena kuti “mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu.”

Kapena kuti “mkulu wa operekera chikho.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “Kudutsitsa pamoto.”

Mawu akuti “kuwombeza” akutanthauza kufuna kudziwa zam’tsogolo, kapena kufufuza ngati zochitika kapena zinthu zinazake zikulosera kuti m’tsogolo mudzachitika zabwino kapena zoipa.

Mawu ake enieni, “Adzamva kubayabaya m’makutu mwake.”

Kapena kuti “zikumbutso.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “Asadutsitse pamoto.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kutanthauza kum’mwera, munthu akayang’ana kum’mawa.

Kutanthauza phiri la Maolivi, makamaka mbali ya kumadzulo kwenikweni, yomwe imatchedwanso kuti phiri la Chokwiyitsa.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Kapena kuti “anaika mpando wake wachifumu pamwamba.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena