Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Ezekiel 1:1-48:35
  • Ezekieli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ezekieli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Ezekieli

Ezekieli

1 M’chaka cha 30, m’mwezi wachinayi, pa tsiku lachisanu la mweziwo, pamene ndinali pakati pa anthu amene anali ku ukapolo+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara,+ kumwamba kunatseguka+ ndipo ndinayamba kuona masomphenya a Mulungu.+ 2 Pa tsiku lachisanu la mweziwo, m’chaka chachisanu kuchokera pamene Mfumu Yehoyakini anatengedwa ukapolo,+ 3 Yehova analankhula+ ndi Ezekieli,+ mwana wa wansembe Buzi, pamene anali m’dziko la Akasidi+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Dzanja la Yehova linafika pa iye kumeneko.+

4 Ndinayamba kuona masomphenya, ndipo ndinaona mphepo yamkuntho+ ikuchokera kumpoto. Ndinaonanso mtambo waukulu+ ndi moto walawilawi.+ Mtambowo unali wowala ndipo unali kuwalitsa malo onse ozungulira pamenepo. Pakati pa motowo panali powala ngati siliva wosakanikirana ndi golide, wooneka ngati akuchokera pakati pa motowo.+ 5 Pakati pa motowo panali zinazake zooneka ngati zamoyo zinayi,+ ndipo zamoyozo zinali zooneka ngati anthu. 6 Chamoyo chilichonse chinali ndi nkhope zinayi+ ndi mapiko anayi.+ 7 Mapazi awo anali owongoka, ndipo kupansi kwa mapazi awo kunali ngati kupansi kwa mapazi a mwana wa ng’ombe.+ Mapaziwo anali kuwala ngati mkuwa wopukutidwa bwino.+ 8 Kunsi kwa mapiko anayi a zamoyozo kunali manja a munthu.+ Zamoyozo zinali ndi nkhope ndiponso mapiko.+ 9 Mapiko a chamoyo china anali kukhudzana ndi a chamoyo china. Zamoyozo sizinali kutembenuka zikamayenda. Chilichonse chinkangopita kutsogolo basi.+

10 Ponena za maonekedwe a nkhope zawo, zamoyo zinayi zimenezi zinali ndi nkhope ya munthu,+ nkhope ya mkango+ mbali ya kumanja,+ nkhope ya ng’ombe yamphongo+ mbali ya kumanzere,+ ndiponso nkhope ya chiwombankhanga.+ 11 Umu ndi mmene nkhope zawo zinalili. Mapiko awo+ anali otambasukira m’mwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri ogundana, ndipo mapiko ena awiri anali kuphimba matupi awo.+

12 Chamoyo chilichonse chinkapita kutsogolo basi.+ Zamoyozo zinali kupita kulikonse kumene mzimu wafuna kuti zipite.+ Zikamayenda sizinali kutembenuka.+ 13 Zamoyozo zinali zooneka ngati makala oyaka moto.+ Pakati pa zamoyozo panali zinazake zooneka ngati miyuni ya moto+ zimene zinali kuyenda uku ndi uku. Motowo unali wowala, ndipo m’motowo munali kutuluka mphezi.+ 14 Zamoyozo zinali kuyenda uku ndi uku, ndipo zikamayenda zinali kuoneka ngati mphezi.+

15 Pamene ndinali kuyang’ana zamoyozo, ndinangoona kuti pansi panali wilo limodzi pafupi ndi zamoyozo,+ pambali pa nkhope zinayi za chamoyo chilichonse.+ 16 Maonekedwe a mawilowo+ anali ngati kuwala kwa mwala wa kulusolito,+ ndipo mawilo anayiwo anali ofanana. Kapangidwe kake kanali ngati kuti wilo lina lili pakati pa wilo linzake.*+ 17 Mawilowo akamayenda, anali kulowera kumbali zonse zinayi+ ndipo sanali kukhotera kwina.+ 18 Malimu a mawilowo anali aatali kwambiri moti anali ochititsa mantha. Malimu anayi onsewo anali odzaza ndi maso.+ 19 Zamoyo zija zikamayenda, mawilowo anali kuyenda pambali pawo. Zamoyozo zikanyamuka kuchoka pansi, mawilowonso anali kunyamuka.+ 20 Kulikonse kumene mzimu ukufuna kupita, zamoyozo zinali kupita kumeneko, chifukwa mzimuwo wafuna kuti upite kumeneko. Mawilowo anali kukwera m’mwamba ali pambali pa zamoyozo, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo. 21 Zamoyozo zikamayenda, mawilowo analinso kuyenda. Zikaima chilili, mawilowonso anali kuima chilili. Zamoyozo zikakwera m’mwamba kuchoka pansi, mawilowonso anali kukwera m’mwamba ali pambali pa zamoyozo, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo.+

22 Pamwamba pa mitu ya zamoyozo, panali chinachake chooneka ngati thambo,+ chonyezimira ngati madzi oundana ochititsa chidwi, choyalidwa pamwamba pa mitu yawo.+ 23 Pansi pa thambolo, mapiko awo anali otambasuka. Phiko lililonse linagundana ndi phiko la chamoyo chinzake. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri ochiphimba mbali imodzi, ndi mapiko ena awiri ochiphimba mbali ina ya thupi lake. 24 Ndinamva phokoso la mapiko awo, lokhala ngati phokoso la madzi ambiri,+ ndiponso ngati phokoso la Wamphamvuyonse. Zikamayenda, zinali kuchita phokoso ngati la chipwirikiti cha anthu,+ ngati phokoso la pamsasa.+ Zikaima chilili, zinali kutsitsa mapiko awo.

25 Pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu yawo, panamveka mawu. (Zikaima chilili, zinali kutsitsa mapiko awo.) 26 Pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu yawo, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro,+ chooneka ngati mpando wachifumu.+ Pachinthu chooneka ngati mpando wachifumucho, panali winawake wooneka ngati munthu,+ atakhala pamwamba pake. 27 Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide,+ chooneka ngati kuti mkati mwake monse mukuyaka moto.+ Kuchokera pa chimene chinali kuoneka ngati chiuno chake kupita m’mwamba ndiponso kutsika m’munsi, munthuyo anali kuoneka ngati moto, ndipo pamalo onse omuzungulira panali powala. 28 Panali chinachake chooneka ngati utawaleza+ umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunali kuonekera. Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.

2 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ imirira kuti ndikulankhule.”+ 2 Atayamba kulankhula nane, mzimu unalowa mwa ine+ ndipo unandiimiritsa kuti ndimvetsere yemwe anali kulankhula ndi ineyo.+

3 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndikukutumiza kwa ana a Isiraeli,+ kwa mitundu yopanduka imene yandipandukira.+ Iwo ndi makolo awo akhala akuphwanya malamulo anga mpaka lero.+ 4 Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ 5 Kaya iwowo akamvetsera+ kapena ayi,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka,+ adzadziwabe kuti pakati pawo panali mneneri.+

6 “Iwe mwana wa munthu, usawaope.+ Usaope mawu awo ngakhale kuti iwo ndi anthu osamva+ ndipo ali ngati zinthu zokulasa.+ Usaope, ngakhale kuti ukukhala pakati pa zinkhanira.+ Usaope mawu awo+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+ 7 Ukawauze mawu anga, kaya akamva kapena ayi, pakuti iwo ndi anthu opanduka.+

8 “Iwe mwana wa munthu, imva zimene ndikukuuza. Usapanduke ngati nyumba yopandukayi.+ Tsegula pakamwa pako kuti udye zimene ndikukupatsa.”+

9 Ndili mkati moyang’ana, ndinangoona dzanja litatambasukira kwa ine.+ M’dzanjalo munali mpukutu wolembedwa.+ 10 Iye anautambasula pamaso panga, ndipo unalembedwa kuseri n’kuseri.+ Mumpukutumo munalembedwa nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira.+

3 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene chili pamaso pakochi. Idya mpukutuwu,+ kenako upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.”

2 Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga, ndipo iye anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.+ 3 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsawu, kuti mimba yako ikhute ndiponso kuti mpukutuwo udzaze m’matumbo mwako.” Choncho ndinayamba kudya mpukutuwo, ndipo unali wotsekemera* ngati uchi m’kamwa mwanga.+

4 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, pita pakati pa nyumba+ ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga. 5 Pakuti sindikukutuma kwa anthu olankhula chinenero chovuta kumva+ ndiponso a lilime lolemera.+ Koma ndikukutuma kunyumba ya Isiraeli, 6 osati kwa mitundu yambiri ya anthu olankhula chinenero chovuta kumva kapena a lilime lolemera, amene sungathe kumvetsetsa mawu awo.+ Ndikanakhala kuti ndinakutuma kwa anthu amenewo, akanakumvera.+ 7 Koma a nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvera, chifukwa iwo safuna kundimvera.+ Pakuti anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani ndi osamva.+ 8 Koma ndachititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo,+ ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+ 9 Ndachititsa chipumi chako kukhala ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope,+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.”+

10 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza,+ ndipo umve ndi makutu ako. 11 Pita pakati pa anthu otengedwa ukapolo,+ pakati pa ana a anthu a mtundu wako, ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena,’ kaya akamve kapena ayi.”+

12 Kenako mzimu unanditenga+ ndipo kumbuyo kwanga ndinayamba kumva mawu amphamvu ngati chimkokomo chachikulu,+ akuti: “Utamandike ulemerero wa Yehova kumalo ake.”+ 13 Kenako ndinamva phokoso la mapiko a zamoyo amene anali kukhulana pafupipafupi.+ Ndinamvanso phokoso la mawilo amene anali pambali pawo,+ ndi chimkokomo chachikulu. 14 Mzimu unandinyamula+ moti ndinapita ndili wachisoni ndi wokwiya kwambiri mumtima mwanga, ndipo dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu.+ 15 Chotero ndinapita kwa anthu otengedwa ukapolo amene anali ku Tele-abibu, amene anali kukhala+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Ndinayamba kukhala pamalo pamene anthuwo anali kukhala ndipo ndinakhala pamenepo masiku 7. Ndinangokhala phee pakati pawo, ndili m’maganizo.+

16 Pamapeto pa masiku 7, Yehova analankhula nane, kuti:

17 “Iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Umve mawu ochokera pakamwa panga ndipo undichenjezere anthuwo.+ 18 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’+ iwe osamulankhula munthu woipayo ndi kumuchenjeza kuti asiye njira yake yoipa n’cholinga choti akhalebe ndi moyo,+ iyeyo poti ndi woipa adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera m’manja mwako.+ 19 Koma iweyo ukachenjeza munthu woipa,+ koma iye osasiya zoipa zakezo ndi njira zake zoipa, munthuyo adzafa chifukwa cha zoipa zake.+ Koma iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.+ 20 Munthu wolungama akasiya chilungamo chake+ n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ine n’kumuikira chopunthwitsa pamaso pake,+ iyeyo adzafa chifukwa chakuti sunamuchenjeze. Adzafa chifukwa cha tchimo lake+ ndipo zinthu zolungama zimene anachita sizidzakumbukiridwa,+ koma magazi ake ndidzawafuna kwa iweyo.+ 21 Koma ngati iweyo unachenjeza munthu wolungama kuti asachimwe,+ iye osachimwadi, munthuyo adzakhalabe ndi moyo chifukwa anachenjezedwa,+ ndipo iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.”+

22 Kenako dzanja la Yehova linafika pa ine kumeneko ndipo iye anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kuchigwa+ ndipo ndikalankhula nawe kumeneko.” 23 Chotero ndinanyamuka n’kupita kuchigwako. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova waimirira,+ ngati ulemerero umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ 24 Kenako mzimu unalowa mwa ine+ n’kundiimiritsa,+ ndipo Mulungu anayamba kulankhula nane, kuti:

“Pita ukadzitsekere m’nyumba mwako. 25 Tsopano iwe mwana wa munthu, dziwa kuti adzakumanga ndi zingwe kuti usapite pakati pawo.+ 26 Ndidzachititsa lilime lako kumatirira kumwamba m’kamwa mwako,+ ndipo sudzathanso kulankhula.+ Sudzakhalanso munthu wowadzudzula,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+ 27 Ndikamalankhula nawe ndizikutsegula pakamwa. Ndiyeno iweyo uzikawauza kuti,+ ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ Wakumva amve,+ ndipo wosamva asamve, pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+

4 “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike pamaso pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu.+ 2 Uchite nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso chiunda chomenyerapo nkhondo*+ ndi misasa yokhalamo asilikali ankhondo. Uikenso zida zankhondo zowonongera mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+ 3 Utenge chiwaya kuti chikhale ngati khoma lachitsulo pakati pa iweyo ndi mzindawo. Uziyang’anitsitsa mzindawo ndipo usonyeze zimene adani adzachite poukira mzindawo. Chimenechi chikhale chizindikiro kwa nyumba ya Isiraeli.+

4 “Iweyo ugonere kumanzere kwako ndipo ugonere zolakwa za nyumba ya Isiraeli.+ Kwa masiku amene udzagonere kumanzereko, udzanyamula zolakwa zawo. 5 Ine ndidzakupatsa zaka zimene iwo akhala akundilakwira+ zokwanira masiku 390,+ ndipo iweyo udzanyamula zolakwa za nyumba ya Isiraeli. 6 Udzakwanitse masiku onsewo.

“Kenako udzagonere mbali ya kumanja kwako, ndipo udzanyamule zolakwa za nyumba ya Yuda kwa masiku 40.+ Tsiku limodzi limene ndakupatsa likuimira chaka chimodzi. Tsiku limodzi kuimira chaka chimodzi.+ 7 Nkhope yako izidzayang’anitsitsa Yerusalemu atazunguliridwa ndi asilikali.+ Udzapinde malaya ako kuti dzanja lako lidzakhale pamtunda, ndipo udzalosere zinthu zoipira mzindawo.

8 “Ine ndidzakumanga ndi zingwe+ kuti usatembenukire kumbali ina, mpaka utamaliza masiku ako ozungulira mzindawo.

9 “Tenga tirigu,+ balere, nyemba zikuluzikulu,+ mphodza,+ mapira, ndi tirigu wamtundu wina.*+ Zonsezo uziike mumphika umodzi kuti zikhale chakudya chako cha masiku amene udzakhale ukugonera mbali imodzi. Udzadye chakudya chimenechi kwa masiku 390.+ 10 Uzidzadya chakudya chochita kuyeza. Tsiku lililonse uzidzadya chokwana masekeli* 20.+ Uzidzadya chakudyachi mwa apo ndi apo.

11 “Uzidzamwa madzi ochita kuyeza, okwanira gawo limodzi la magawo 6 a muyezo wa hini.* Tsiku lililonse, uzidzamwa madziwa nthawi ndi nthawi.

12 “Uzidzadya chakudyacho ngati mkate wozungulira wa balere+ ndipo uzidzachiphika pa tudzi+ touma ta anthu, iwo akuona.” 13 Yehova anapitiriza kunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ana a Isiraeli azidzadya chakudya chodetsedwa+ pakati pa mitundu yosiyanasiyana imene ndidzawathamangitsireko.”+

14 Kenako ine ndinati: “Chonde Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindine woipitsidwa.+ Sindinadyepo nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo kuyambira ndili mwana+ mpaka panopo, ndipo m’kamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+

15 Choncho iye anandiuza kuti: “Chabwino, ndikupatsa ndowe za ng’ombe m’malo mwa tudzi touma ta anthu kuti uphikirepo chakudya chako.” 16 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola ndodo mu Yerusalemu. Ndidzathyola ndodo zimene amakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+ Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa.+ Iwo adzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha,+ 17 mwakuti chakudya ndi madzi zidzakhala zosowa. Azidzayang’anizana modabwa ndipo adzaonda chifukwa cha zolakwa zawo.+

5 “Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa. Likhale ngati lezala lako lometela ndipo umetele tsitsi lako ndi ndevu zako.+ Kenako utenge sikelo yoyezera ndipo ugawe tsitsilo m’magawo atatu. 2 Gawo limodzi la magawo atatu a tsitsilo ulitenthe pamoto pakati pa mzindawo masiku ozungulira mzindawo akatha.+ Kenako utenge gawo lina la magawo atatuwo. Gawo limeneli uzilimenya ndi lupanga ukuzungulira mzinda wonsewo.+ Gawo lomaliza la magawo atatuwo uliuluze ndi mphepo ndipo ine ndidzalitsatira nditasolola lupanga.+

3 “Pagawo lachitatuli utengepo tsitsi lochepa n’kulikulunga m’zovala zako.+ 4 Utengeponso tsitsi lina n’kuliponya pamoto kuti linyeke. Kuchokera pamoto umenewu, padzabuka moto umene udzafalikire kunyumba yonse ya Isiraeli.+

5 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa mitundu ya anthu ndipo wazunguliridwa ndi mayiko ena. 6 Iye anapandukira zigamulo zanga pochita zoipa zoposa za mitundu ya anthuwo.+ Anapandukiranso malamulo anga kuposa mayiko amene amuzungulira, pakuti iye anakana zigamulo zanga ndipo sanayende m’malamulo anga.’+

7 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti anthu inu munali ovuta+ kuposa mitundu imene yakuzungulirani, ndipo simunayende m’malamulo anga, komanso simunatsatire zigamulo zanga,+ koma munatsatira zigamulo za mitundu imene yakuzungulirani,+ 8 izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena: “Ine ndithana nawe mzinda iwe,+ ndipo ndidzapereka zigamulo pakati pako pamaso pa mitundu ya anthu.+ 9 Chifukwa cha zonyansa zako zonse, ndidzakuchita zimene sindinachitepo ndiponso zimene sindidzachitanso.+

10 “‘“Choncho pakati pako, abambo adzadya ana awo+ ndipo ana adzadya abambo awo. Ine ndidzakulanga ndipo anthu ako onse otsala ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi.”’+

11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+ 12 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzafa ndi mliri+ ndipo adzatha ndi njala pakati pako.+ Gawo lina la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira. Gawo lomaliza la magawo atatu a anthu a mtundu wako ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+ 13 Ndiyeno mkwiyo wanga udzatha+ ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+ Kenako mtima wanga udzakhala pansi.+ Ndikadzathetsera ukali wanga pa iwo, pamenepo iwo adzadziwa kuti ine Yehova ndalankhula chifukwa ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha basi.+

14 “‘Iweyo ndidzakusandutsa malo abwinja. Ndidzakusandutsanso chitonzo pakati pa mitundu yokuzungulira ndi pamaso pa munthu aliyense wodutsa.+ 15 Udzakhala chitonzo+ ndi chinthu chochilankhulira mawu onyoza.+ Udzakhalanso chenjezo+ ndi choopsezera mitundu yokuzungulira ndikadzakuweruza mokwiya komanso mwaukali, ndiponso ndikadzakulanga mokwiya.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.

16 “‘Ndikadzakutumizirani mivi yakupha yobweretsa njala+ imene idzakuwonongeni,+ ndidzachititsa kuti njala ikule pakati panu, ndipo ndidzathyola ndodo zimene mumakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+ 17 Ndidzakutumizirani njala ndi zilombo zakupha+ ndipo zidzakupherani ana anu. Mliri+ ndi magazi+ zidzadutsa pakati panu ndipo ine ndidzakubweretserani lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”

6 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kumapiri a Isiraeli ndipo ulosere+ kwa iwo.+ 3 Unene kuti, ‘Inu mapiri a Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa:+ Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa mapiri, zitunda,+ mitsinje ndi zigwa: “Ine ndidzakubweretserani lupanga ndipo ndidzawononga malo anu okwezeka.+ 4 Maguwa anu ansembe adzasiyidwa.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzaphwanyidwa, ndipo anthu anu ophedwa ndidzawagwetsera pamaso pa mafano anu onyansa.*+ 5 Ndidzaika mitembo ya ana a Isiraeli pamaso pa mafano awo onyansa, ndipo mafupa anu ndidzawamwaza kuzungulira maguwa anu ansembe.+ 6 M’malo anu onse okhala,+ mizinda idzawonongedwa+ ndipo malo okwezeka adzasakazidwa kuti akhale mabwinja ndiponso kuti maguwa anu ansembe akhale osakazidwa.+ Chotero maguwa anu ansembewo adzaphwanyidwa+ ndipo mafano anu onyansa sadzakhalaponso.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa+ ndipo ntchito za manja anu zidzafafanizidwa. 7 Mitembo ya anthu ophedwa a mtundu wanu idzakhala pakati panu,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+

8 “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+ 9 Opulumuka anu akadzagwidwa n’kutengedwa kukakhala pakati pa mitundu ina ya anthu, ndithu adzandikumbukira.+ Adzakumbukira mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha mtima wawo wadama umene unawachititsa kundipandukira.+ Adzakumbukiranso mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha maso awo othamangira mafano awo onyansa pofuna kuchita nawo zadama.+ Iwo adzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zawo, chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+ 10 Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. Sikuti ndangonena pachabe+ zoti ndidzawabweretsera tsoka limeneli.”’+

11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ombani m’manja+ ndipo pondani pansi mwamphamvu ndi mapazi anu. Munene kuti: “Kalanga ine!” chifukwa cha zoipa zonse zonyansa za nyumba ya Isiraeli.+ Pakuti iwo adzaphedwa ndi lupanga,+ njala+ ndi mliri.+ 12 Yemwe ali kutali+ adzaphedwa ndi mliri. Yemwe ali pafupi adzaphedwa ndi lupanga. Yemwe watsala ali wotetezeka adzafa ndi njala, ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+ 13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+ 14 Ndidzawatambasulira dzanja langa powalanga+ ndipo dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja. Malo awo onse okhala adzakhala bwinja loipa kuposa chipululu cha Dibula, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

7 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza dziko la Isiraeli, kuti: ‘Mapeto! Mapeto afika kumalekezero anayi a dzikoli.+ 3 Tsopano mapeto akufikira,+ ndipo ndikutumizira mkwiyo wanga. Ndikuweruza mogwirizana ndi njira zako+ ndipo ndikubwezera chifukwa cha zonyansa zako zonse. 4 Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

5 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsoka! Tsoka loti silinaonekepo likubwera.+ 6 Mapeto akubwera,+ ali m’njira. Akufikira mwadzidzidzi. Akubwera ndithu.+ 7 Nkhata yamaluwa ya tsoka ibwera kwa inu anthu okhala m’dzikoli. Nthawi ikwana. Tsikulo layandikira.+ M’dzikoli muli chisokonezo, osati phokoso lachisangalalo lomveka m’mapiri.

8 “‘Posachedwapa, ndikukhuthulirani ukali wanga,+ ndipo mkwiyo wanga ndiuthetsera pa inu.+ Ndikuweruzani mogwirizana ndi njira zanu,+ ndipo ndikubwezerani chifukwa cha zonyansa zanu zonse. 9 Diso langa silidzakumverani chisoni+ ndipo sindidzakuchitirani chifundo.+ Ndidzakubwezerani mogwirizana ndi njira zanu, ndipo mudzaona zotsatirapo za zinthu zanu zonyansa zimene zili pakati panu.+ Ndiyeno anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, amene ndikukuphani.+

10 “‘Taona! Tsikulo likubwera.+ Nkhata yamaluwa ya tsoka ili m’njira.+ Ndodo yachita maluwa.+ Kudzikuza kwaphuka.+ 11 Chiwawa chasanduka ndodo ya zoipa.+ Anthuwo paokha, chuma chawo, ndiponso kutchuka kwawo, sizidzawapulumutsa ku chilango. 12 Nthawi idzakwana, tsikulo lidzafika. Wogula asasangalale+ ndipo wogulitsa asalire, pakuti mkwiyo wa Mulungu wayakira khamu lonselo. 13 Wogulitsa sadzabwerera ku chinthu chimene chinagulitsidwa akadali ndi moyo, pakuti masomphenyawo ndi akhamu lonselo. Palibe amene adzabwerere kapena kukhalabe ndi moyo kudzera m’zolakwa zake.

14 “‘Iwo aliza lipenga+ ndipo aliyense wakonzeka, koma palibe amene akupita kunkhondo chifukwa mkwiyo wanga wayakira khamu lonselo.+ 15 Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+ 16 Anthu awo opulumuka adzathawa+ ndipo adzakhala pamapiri ngati njiwa za m’zigwa,+ aliyense akulira chifukwa cha zolakwa zake. 17 Anthu onse ataya mtima+ ndipo mawondo onse akungochucha madzi.*+ 18 Iwo avala ziguduli,*+ ndipo thupi lawo lonse likunjenjemera.+ Pankhope zawo zonse pali manyazi+ ndipo m’mitu yawo yonse muli mipala.+

19 “‘Siliva wawo adzamuponyera mumsewu ndipo golide wawo adzaipidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa m’tsiku la mkwiyo waukulu wa Yehova.+ Iwo sadzakhuta ndipo m’matumbo mwawo simudzadzaza, pakuti chumacho chakhala chowapunthwitsa ndiponso chowachititsa zolakwa.+ 20 Aliyense akunyada chifukwa cha chinthu chake chokongoletsera. Iwo agwiritsira ntchito siliva ndi golide kupangira mafano awo onyansa,+ ndi zinthu zawo zonyansa.+ N’chifukwa chake ndidzachititse kuti zinthu zimenezi adzaipidwe nazo.+ 21 Ndidzazipereka m’manja mwa alendo kuti zikhale zawo ndi kwa anthu oipa a padziko lapansi kuti azitenge,+ ndipo adzaziipitsa.

22 “‘Ine ndidzatembenuza nkhope yanga kuti ndisawayang’ane+ ndipo adzaipitsa malo anga obisika. Akuba adzalowa m’malowo n’kuipitsamo.+

23 “‘Panga unyolo+ chifukwa dzikolo ladzaza ziweruzo za magazi,+ ndipo mumzindamo mwadzaza chiwawa.+ 24 Chotero ndidzabweretsa anthu oipa kwambiri a mitundu ina+ ndipo iwo adzalanda nyumba zawo.+ Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu+ ndipo malo awo opatulika adzaipitsidwa.+ 25 Anthu adzazunzika, adzafunafuna mtendere koma sudzapezeka.+ 26 M’dzikolo mudzakhala mavuto otsatizanatsatizana+ ndipo muzidzamveka mauthenga otsatizanatsatizana. Anthu azidzafunafuna masomphenya kwa mneneri.+ Ansembe sadzathanso kuphunzitsa malamulo aphindu. Anthu achikulire sadzaperekanso malangizo othandiza.+ 27 Mfumu idzalira,+ ndipo ngakhale mtsogoleri adzagwidwa ndi mantha.+ Manja a anthu a m’dzikolo adzanjenjemera chifukwa cha chisokonezo. Ndidzawachitira zinthu zogwirizana ndi njira zawo.+ Ndidzawaweruza mogwirizana ndi ziweruzo zawo.+ Chotero iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

8 M’chaka cha 6, m’mwezi wa 6, pa tsiku lachisanu la mweziwo, ndinali nditakhala m’nyumba mwanga ndipo akuluakulu a Yuda anali atakhala pamaso panga.+ Pamenepo, dzanja la Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, linafika pa ine.+ 2 Ndinayamba kuona masomphenya ndipo ndinaona winawake wooneka ngati moto.+ Kuchokera pa chimene chinali kuoneka ngati chiuno chake kupita m’munsi, panali moto.+ Kuchokera m’chiuno mwake kupita m’mwamba, panali chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+ 3 Kenako iye anatambasula chinachake chooneka ngati dzanja+ ndipo anagwira tsitsi la kumutu kwanga n’kundinyamula. Ndiyeno mzimu+ unandinyamulira m’malere, pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, n’kundipititsa ku Yerusalemu m’masomphenya a Mulungu.+ Unandifikitsa pakhomo la kanyumba ka pachipata cha bwalo lamkati+ choyang’ana kumpoto. Pamenepo m’pamene panali kukhala chizindikiro choimira nsanje, chimene chinali kuchititsa Mulungu nsanje.+ 4 Kumeneko ndinaonako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli,+ wofanana ndi zimene ndinaona kuchigwa zija.

5 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, takweza maso ako uyang’ane kumpoto.” Chotero ndinakweza maso anga n’kuyang’ana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa chipata cha guwa lansembe kunali chizindikiro choimira nsanje+ pakhomo la chipatalo. 6 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zonyansa kwambiri zimene anthuwa akuchita?+ Ukuona kodi zinthu zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akundichitira kunoko kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri.”

7 Kenako anandipititsa pakhomo lolowera m’bwalo lamkati, ndipo ndinaona kuti pakhoma* panali chibowo. 8 Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, taboola khomalo.”+ Ine ndinabooladi khomalo ndipo ndinangoona kuti panalinso khomo lina. 9 Kenako iye anandiuza kuti: “Lowa uone zinthu zoipa ndi zonyansa zimene anthu akuchita kuno.”+ 10 Chotero ine ndinalowa, ndipo ndinaona kuti pamakoma anajambulapo zithunzi+ za nyama iliyonse yokwawa, za chilombo chilichonse chonyansa+ ndi za mafano onse onyansa a nyumba ya Isiraeli.+ Pamakoma onse anajambulapo zithunzizo mochita kugoba. 11 Ndinaonanso akuluakulu 70+ a nyumba ya Isiraeli ataimirira. Yaazaniya mwana wa Safani+ anali ataima pakati pawo. Iwo anaima pamaso pa zojambulazo, aliyense atanyamula chiwaya chofukizira nsembe m’manja mwake. Utsi wonunkhira wa zofukizazo unali kukwera m’mwamba.+ 12 Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mu mdima?+ Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita m’chipinda chamkati mmene muli fano lake losema? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona.+ Yehova wachokamo m’dziko muno.’”

13 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri zimene iwo akuchita.”+ 14 Chotero anandipititsa pakhomo la pachipata cha nyumba ya Yehova chimene chili mbali ya kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona amayi atakhala pansi akulirira mulungu wotchedwa Tamuzi.

15 Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimenezi? Uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri+ kuposa zimenezi.” 16 Chotero anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera m’kachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe,+ panali amuna pafupifupi 25+ atafulatira kachisi wa Yehova.+ Nkhope zawo anali atazilozetsa kum’mawa ndipo anali kugwadira dzuwa atayang’ana kum’mawa.+

17 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi a nyumba ya Yuda akuona ngati ndi chinthu chaching’ono kuchita zinthu zonyansa zimene akuchita panozi? Kodi akufunanso kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ n’kundikwiyitsa kachiwiri? Kodi waonanso kuti iwowo akulozetsa nthambi* kumphuno kwanga? 18 Choncho ineyo ndidzachitapo kanthu mwaukali.+ Diso langa silidzawamvera chisoni ndipo sindidzawachitira chifundo.+ Iwo adzandiitana mofuula, koma ine sindidzamva.”+

9 Kenako iye analankhula mokuwa ine ndikumva, kuti: “Uzani anthu amene asankhidwa kuti awononge mzindawu kuti abwere pafupi. Aliyense anyamule chida chake chowonongera.”

2 Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kuchipata chakumtunda+ choyang’ana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chophwanyira. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu.+ M’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati n’kuima pambali pa guwa lansembe lamkuwa.+

3 Tsopano ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi+ pamene unali, ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Kenako Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu wovala zovala zansalu uja,+ yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera. 4 Pamenepo Yehova anauza munthu uja kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu, ndipo ulembe chizindikiro pamphumi za anthu amene akuusa moyo* ndi kubuula+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.”+

5 Ndiyeno iye anauza amuna ena aja ine ndikumva, kuti: “M’tsatireni ameneyu. Muyendeyende mumzindamo n’kumapha anthu. Diso lanu lisamve chisoni ndipo inuyo musachite chifundo.+ 6 Mupheretu nkhalamba, anyamata, anamwali, tiana, ndi amayi.+ Koma musayandikire munthu aliyense amene ali ndi chizindikiro,+ ndipo muyambire pamalo anga opatulika.”+ Chotero iwo anayambira kupha akuluakulu amene anali panyumbapo.+ 7 Iye anawauzanso kuti: “Ipitsani nyumbayi ndipo mudzaze mabwalo ake ndi mitembo ya anthu ophedwa.+ Pitani!” Iwo anapitadi n’kukapha anthu mumzindamo.

8 Pamene amunawo anali kupha anthu, ine ndinatsala ndekha wamoyo, ndipo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinafuula kuti: “Kalanga ine,+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi muwononga otsala onse a Isiraeli pamene mukukhuthulira ukali wanu pa Yerusalemu?”+

9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+ 10 Chotero inenso diso langa silimva chisoni+ ndipo sindichita chifundo.+ Ndiwabwezera mogwirizana ndi njira zawo.”+

11 Tsopano munthu wovala zovala zansalu uja, yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera, anabwera n’kudzanena kuti: “Ndachita monga momwe munanditumira.”+

10 Ndinapitiriza kuona masomphenya, ndipo ndinaona kuti pamwamba pa thambo+ limene linali pamwamba pa mitu ya akerubi, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro.+ Chinthucho chinalinso chooneka ngati mpando wachifumu,+ ndipo chinali kuonekera pamwamba pa mitu yawo. 2 Kenako Mulungu anauza munthu amene anavala zovala zansalu+ uja, kuti: “Pita pakati pa mawilo,+ pansi pa akerubi. Ukatengepo makala+ amoto odzaza manja ako onse awiri kuchokera pakati pa akerubiwo, ndipo ukawaponye pamzindawo.”+ Chotero iye anapitadi ine ndikuona.

3 Akerubiwo anali ataimirira mbali ya kumanja kwa nyumbayo pamene munthuyo anapita pakati pawo, ndipo mtambo unali utadzaza bwalo lonse lamkati.+ 4 Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo. 5 Phokoso la mapiko a akerubiwo+ linali kumveka mpaka kubwalo lakunja. Phokosolo linali kumveka ngati kulankhula kwa Mulungu Wamphamvuyonse.+

6 Kenako Mulungu analamula munthu wovala zovala zansalu uja kuti: “Tenga moto pakati pa mawilo, pakati pa akerubi.” Atatero munthuyo anapita n’kukaima pambali pa wilo. 7 Ndiyeno kerubi wina anatambasula dzanja lake kuchokera pakati pa akerubiwo n’kutapa moto+ umene unali pakati pawo.+ Iye anatenga motowo n’kuuika m’manja mwa munthu wovala zovala zansalu+ uja, ndipo munthuyo anatenga motowo n’kuchoka. 8 Kupansi kwa mapiko a akerubiwo,+ kunaoneka chinachake chokhala ngati dzanja la munthu.

9 Ndinapitiriza kuona masomphenya, ndipo ndinaona kuti pambali pa akerubi panali mawilo anayi. Pambali pa kerubi aliyense panali wilo limodzi.+ Maonekedwe a mawilowo anali ngati kuwala kwa mwala wa kulusolito. 10 Mawilo anayiwo anali ofanana. Anali kuoneka ngati kuti wilo lina lili pakati pa wilo linzake.*+ 11 Mawilowo anali kulowera kumbali zawo zonse zinayi. Akamayenda, sanali kukhota chifukwa chakuti anali kulowera kumene mitu ya akerubiwo* yayang’ana. Akamayenda sanali kukhota.+ 12 Zamoyozo zinali ndi maso paliponse. Zinali ndi maso pamatupi awo, kumbuyo kwawo, m’manja awo, m’mapiko awo, ndiponso kuzungulira mawilo onse.+ Pambali pa kerubi aliyense mwa akerubi anayi amenewo, panali wilo. 13 Kenako ndinamva mawu akuitana mawilowo kuti, “Mawilo inu!”

14 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi.+ Nkhope yoyamba inali ya kerubi. Nkhope yachiwiri inali ya munthu.+ Nkhope yachitatu inali ya mkango, ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.+

15 Akerubiwo anali zamoyo zomwe zija zimene ndinaziona kumtsinje wa Kebara.+ Akerubiwo akanyamuka kukwera m’mwamba,+ 16 kapena akamapita, mawilo aja anali kupita nawo limodzi ali pambali pawo.+ Akerubiwo akatambasula mapiko awo kuti akhale pamwamba pa dziko lapansi, mawilo sanali kutembenukira kwina, anali kungokhala pambali pa zamoyozo.+ 17 Akerubi akaima chilili, mawilonso anali kuima chilili. Akerubiwo akakwera m’mwamba,+ mawilonso anali kukwera m’mwamba, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo.+

18 Kenako ulemerero+ wa Yehova unanyamuka kuchoka pakhomo la nyumba yopatulika n’kukakhala pamwamba pa akerubi.+ 19 Tsopano akerubi aja anatambasula mapiko awo n’kunyamuka kuchoka pansi+ ine ndikuona. Atanyamuka, mawilo aja anali pambali pawo. Kenako iwo anakaima pakhomo la kum’mawa la chipata cha nyumba ya Yehova, ndipo ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo.

20 Zimenezi zinali zamoyo+ zimene ndinaziona pansi pa mpando wachifumu wa Mulungu wa Isiraeli kumtsinje wa Kebara,+ choncho ndinadziwa kuti anali akerubi. 21 Pa zamoyo zinayizo, chamoyo chilichonse chinali ndi nkhope zinayi+ ndi mapiko anayi, ndipo kupansi kwa mapiko awo kunali zinthu zooneka ngati manja a munthu. 22 Nkhope zawo zinali zofanana ndi zimene ndinaziona m’mphepete mwa mtsinje wa Kebara. Zinali zofanana ndendende.+ Chamoyo chilichonse chinali kupita kutsogolo basi.+

11 Kenako mzimu+ unandinyamula+ n’kupita nane kuchipata cha kum’mawa cha nyumba ya Yehova chimene chinayang’ana mbali ya kum’mawa.+ Pakhomo la chipatacho ndinaonapo amuna okwanira 25.+ Pakati pawo ndinaonapo Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Amuna onsewo anali akalonga.+ 2 Ndiyeno Mulungu anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, amuna amenewa ndi amene akukonza chiwembu, ndiponso amene akukonza zoipa zokhudza mzindawu.+ 3 Iwo akunena kuti: ‘Ino ndiyo nthawi yomanga nyumba.+ Mzindawu uli ngati mphika wakukamwa kwakukulu,+ ndipo ifeyo tili ngati nyama mumphikamo.’

4 “Tsopano iweyo, losera zinthu zowaipira. Losera, iwe mwana wa munthu.”+

5 Kenako mzimu wa Yehova unafika pa ine,+ ndipo iye anandiuza kuti: “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Inu anthu a nyumba ya Isiraeli, mwanena bwino, ndipo ine ndadziwa maganizo anu.+ 6 Inuyo mwapha anthu ambiri mumzindawu komanso mwadzaza misewu yake ndi anthu ophedwa.”’”+ 7 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Anthu ophedwa amene mwawaika pakati pa mzindawu ndiwo nyama.+ Mzindawu ndiwo mphika wakukamwa kwakukulu.+ Koma inuyo mudzatulutsidwa mumzindawu.’”+

8 “‘Inu mukuopa lupanga,+ koma ine ndidzakubweretserani lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 9 ‘Ndithu ine ndidzakutulutsani mumzindawu n’kukuperekani m’manja mwa alendo,+ ndipo ndidzakulangani.+ 10 Inu mudzaphedwa ndi lupanga.+ Ndidzakuweruzirani m’malire a Isiraeli,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 11 Kwa inu, mzindawu sudzakhala mphika wakukamwa kwakukulu+ ndipo inuyo simudzakhala nyama mkati mwa mphikawo. Ndidzakuweruzirani m’malire a Isiraeli. 12 Inuyo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, chifukwa simunasunge malamulo anga ndiponso simunatsatire zigamulo zanga.+ Koma inu munatsatira zigamulo za anthu a mitundu yokuzungulirani.’”+

13 Nditangomaliza kulosera, Pelatiya mwana wa Benaya anamwalira.+ Choncho ine ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi, n’kufuula+ kuti: “Kalanga ine, inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa!+ Kodi mukufuna kufafaniziratu Aisiraeli otsalawa?”+

14 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 15 “Iwe mwana wa munthu, anthu okhala ku Yerusalemu alankhula kwa abale ako+ enieni,* kwa nyumba yonse ya Isiraeli, ndiponso kwa anthu onse, kuti, ‘Chokani, pitani kutali ndi Yehova. Dzikoli ndi lathu. Laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’+ 16 Tsopano uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ngakhale kuti ndakawaika pakati pa mitundu yakutali yosiyanasiyana ya anthu, ndiponso ndawabalalitsira m’mayiko osiyanasiyana,+ ine ndidzakhala malo opatulika kwa iwo kwa kanthawi kochepa, m’mayiko amene iwo akukhalamo.”’+

17 “Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera m’mayiko amene ndinakubalalitsirani, ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.”+ 18 “‘Ndithu iwo adzabwera m’dzikomo, ndipo adzachotsamo mafano onse onyansa ndi zinthu zonse zonyansa.+ 19 Ndidzawapatsa mtima umodzi+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo.+ Ndidzachotsa mtima wamwala m’matupi awo+ n’kuwapatsa mtima wamnofu,+ 20 kuti azidzatsatira malamulo anga, azidzasunga zigamulo zanga ndi kuzikwaniritsa.+ Iwo adzakhaladi anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”’+

21 “‘“Koma amene akuumirira mafano awo onyansa ndi zinthu zawo zonyansa,+ ndidzawabwezera monga mwa njira zawo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+

22 Tsopano akerubi+ aja anatambasula mapiko awo ndipo mawilo anali pambali pawo.+ Ulemerero+ wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pa mitu yawo.+ 23 Kenako, ulemerero wa Yehova+ unakwera m’mwamba kuchoka pakati pa mzindawo, n’kukaima pamwamba pa phiri+ limene lili kum’mawa kwa mzindawo.+ 24 Tsopano mzimu+ unandinyamula+ n’kukandisiya kudziko la Kasidi kumene kunali anthu ogwidwa ukapolo.+ Zimenezi zinachitika m’masomphenya amene ndinaona mwa mzimu wa Mulungu. Kenako masomphenya amene ndinaonawa anachoka pa ine. 25 Pambuyo pake, ndinayamba kuuza anthu ogwidwa ukapolowo zinthu zonse za Yehova zimene iye anandionetsa.+

12 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka+ omwe ali ndi maso koma saona,+ omwe ali ndi makutu koma samva,+ chifukwa ndi anthu opanduka.+ 3 Tsopano iweyo mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo ndipo upite ku ukapolo masana, anthu akuona. Upite ku ukapolo iwo akuona. Uchoke kwanu kupita kumalo ena. Mwina azindikira tanthauzo lake ngakhale kuti iwo ndi anthu opanduka.+ 4 Utulutse katundu wako monga katundu wopita naye ku ukapolo. Umutulutse masana iwo akuona. Madzulo, iweyo unyamuke iwo akuona. Unyamuke ngati mmene amachitira anthu otengedwa kupita ku ukapolo.+

5 “Uboole khoma iwo akuona n’kutulutsirapo katundu wako.+ 6 Unyamule katunduyo paphewa iwo akuona, ndipo utulutse katunduyo kuli mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone dziko chifukwa ndakuika kuti ukhale chizindikiro+ kwa nyumba ya Isiraeli.”+

7 Chotero ine ndinachita zonse monga mmene anandilamulira.+ Ndinatulutsa katundu wanga masana ngati mmene amachitira anthu opita ku ukapolo. Madzulo ndinaboola khoma ndi manja. Kutagwa mdima, ndinatulutsa katundu wanga, ndipo ndinanyamula katunduyo paphewa iwo akuona.

8 M’mawa Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 9 “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu opanduka a nyumba ya Isiraeli+ sanakufunse kuti, ‘Kodi ukuchita chiyani?’ 10 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali uthenga uwu wotsutsana ndi mtsogoleri,+ uthenga wokhudza Yerusalemu ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli amene ali kumeneko.”’

11 “Uwauze kuti iweyo ndiwe chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ kwa iwo. Zidzachitika kwa iwo monga mmene iwe wachitira. Iwo adzapita ku ukapolo, kudziko lina.+ 12 Mtsogoleri amene ali pakati pawo adzanyamula katundu wake paphewa n’kumapita mu mdima. Adzaboola khoma n’kutulukirapo.+ Iye adzaphimba kumaso kuti asaone dziko. 13 Ine ndidzamutambasulira ukonde wanga. Chotero iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira+ ndipo ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi.+ Koma iye sadzaliona ndipo adzafera komweko.+ 14 Anthu onse omuzungulira amene amamuthandiza, ndiponso magulu ake onse ankhondo, ndidzawabalalitsira ku mphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+ 15 Ndikadzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndi kumayiko ena, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 16 Pakati pawo ndidzapulumutsapo amuna ochepa kuti asaphedwe ndi lupanga,+ njala, kapena miliri, n’cholinga chakuti akafotokoze za zinthu zawo zonse zonyansa+ pakati pa mitundu imene akakhaleko,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”

17 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, idya chakudya ukunjenjemera, ndipo umwe madzi ndi mantha ndiponso nkhawa.+ 19 Anthu a m’dzikoli uwauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa anthu okhala mu Yerusalemu, okhala m’dziko la Isiraeli:+ “Adzadya chakudya ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ndi mantha, pakuti dzikolo lidzakhala bwinja.+ Zinthu zonse za mmenemo zidzachotsedwa chifukwa cha zinthu zachiwawa zimene anthu onse okhala mmenemo akuchita.+ 20 Mizinda ya anthu idzawonongedwa.+ Dzikolo lidzangokhala bwinja lokhalokha,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+

21 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene anthu inu okhala m’dziko la Isiraeli mukunena+ wakuti, ‘Masiku akupita+ koma palibe masomphenya amene akwaniritsidwa,’+ umatanthauza chiyani? 23 Chotero uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndithu Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’+ Koma uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo zonse zotchulidwa m’masomphenya zichitikadi.’ 24 Pakati pa nyumba ya Isiraeli sipadzakhalanso masomphenya opanda pake+ kapena kulosera kwachiphamaso.+ 25 ‘“Pakuti ine Yehova ndidzalankhula, ndipo mawu amene ndidzalankhulewo adzakwaniritsidwadi.+ Sindidzazengerezanso+ chifukwa ine ndidzalankhula mawu m’masiku anu,+ inu a m’nyumba yopanduka, ndipo mawuwo ndidzawakwaniritsa,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”

26 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 27 “Iwe mwana wa munthu, a nyumba ya Isiraeli akunena kuti, ‘Masomphenya amene akuona adzachitika m’tsogolo, ndipo akulosera zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo kwambiri.’+ 28 Chotero iwe uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Sindidzazengerezanso pa zimene ndalankhula.+ Mawu alionse amene ndalankhula adzakwaniritsidwadi,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”+

13 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli.+ Uuze amene akulosera zam’mutu mwawo+ kuti, ‘Mvetserani mawu a Yehova.+ 3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa,+ amene akungolosera zamumtima mwawo+ pamene sanaone chilichonse.+ 4 Iwe Isiraeli, aneneri ako akhala ngati nkhandwe za m’mabwinja.+ 5 Amuna inu, simudzapita kukakhala m’mipata ya mpanda+ kuti mukamenye nkhondo, kapena kuti mukamangire nyumba ya Isiraeli mpanda wamiyala+ n’cholinga chakuti mudzadziteteze pa nkhondo ya m’tsiku la Yehova.”+ 6 “Iwo aona masomphenya abodza ndipo alosera zonama.+ Akunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene Yehova sanawatume, ndipo akuyembekeza kuti zimene anenazo zichitika.+ 7 Amuna inu, kodi masomphenya mwaonawa si abodza? Kodi zimene mwaloserazi si zonama? Inu mwati, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene ine sindinalankhule kalikonse.”’+

8 “‘Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Pakuti amuna inu mwalankhula zabodza ndipo mwaona masomphenya onama, ine ndithana nanu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 9 Dzanja langa lalimbana ndi aneneri amene akuona masomphenya abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzapitiriza kukhala m’gulu la anthu anga apamtima,+ komanso sadzalembedwa m’buku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli.+ Sadzabwera kudziko la Isiraeli+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+ 10 chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” Koma palibe mtendere.+ Palinso munthu amene akumanga khoma lachipinda, ndipo anthu ena akulipaka laimu pachabe.’+

11 “Uza anthu amene akupaka laimuwo kuti khomalo lidzagwa. Kudzagwa mvula yambiri imene madzi ake adzasefukira. Kudzagwa matalala ndipo mphepo yamkuntho idzang’amba khomalo.+ 12 Ndithu khomalo lidzagwa. Amuna inu, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Ali kuti laimu amene munapaka uja?’+

13 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzatumiza mphepo yamkuntho, mvula yambiri ndi matalala, kusonyeza mkwiyo wanga kuti ndikuwonongeni.+ 14 Khoma limene amuna inu mwalipaka laimulo, ndidzaligwetsa lonse mpaka pansi moti maziko ake adzaonekera.+ Mzindawo udzawonongedwa ndithu, ndipo inuyo mudzathera pakati pake. Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

15 “‘Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pakhomalo ndiponso pa anthu amene analipaka laimu. Anthu inu ndidzakuuzani kuti: “Khoma lija kulibe, komanso anthu amene analipaka laimu aja kulibe,+ 16 kutanthauza aneneri a mu Isiraeli amene akulosera zokhudza Yerusalemu, amene akuona masomphenya onena za mzindawo kuti mudzakhala mtendere+ pamene simudzakhala mtendere,”’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

17 “Koma iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kwa ana aakazi a anthu a mtundu wako, amene akulosera+ zam’mutu mwawo+ monga aneneri aakazi, ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire. 18 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa akazi amene akusoka pamodzi zinthu zovala m’zigongono, amenenso akupanga zophimba kumutu za mitu ya anthu otalika mosiyanasiyana n’cholinga chakuti awakole mumsampha anthuwo.+ Kodi mukusaka miyoyo ya anthu anga? Kodi pochita zimenezi, mukuganiza kuti mupulumutsa miyoyo yanu? 19 Kodi zoona mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza m’manja ndi nyenyeswa za mkate?+ Kodi mukuphadi anthu osayenera kufa,+ ndipo mukusiya anthu osayenera kukhala ndi moyo, ponamiza anthu anga amene akumva bodza lanulo?”’+

20 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi zovala za m’mikono za akazi inu, zimene mukukolera miyoyo ya anthu ngati kuti ndi mbalame. Ine ndizichotsa m’mikono mwanu ndi kumasula miyoyo ya anthu imene mukuikola ngati mbalame.+ 21 Nding’amba zovala zanu zakumutu ndi kulanditsa anthu anga m’manja mwanu, ndipo iwo sadzakhalanso m’manja mwanu ngati zinthu zogwidwa posaka. Chotero inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 22 Chifukwa chakuti mwakhumudwitsa mtima wa munthu wolungama mwa chinyengo chanu,+ pamene ineyo sindinamukhumudwitse, ndiponso chifukwa chakuti mwalimbitsa manja a munthu woipa+ kuti asasiye njira zake zoipa, n’kukhala ndi moyo,+ 23 akazi inu simupitiriza kuona masomphenya abodza+ ndipo simudzaloseranso zam’tsogolo.+ Ineyo ndidzapulumutsa anthu anga m’manja mwanu+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

14 Tsopano akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine n’kudzakhala pamaso panga.+ 2 Kenako Yehova analankhula nane kuti: 3 “Iwe mwana wa munthu, amuna awa aika mitima yawo pamafano onyansa, ndipo aika pamaso pawo chinthu chopunthwitsa chimene chimawalakwitsa.+ Kodi ndiwayankhe iwo akamandifunsa?+ 4 Chotero lankhula nawo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli amene waika mtima wake pamafano ake onyansa+ ndiponso amene waika pamaso pake chinthu chopunthwitsa chimene chimamulakwitsa n’kupita kwa mneneri, ine Yehova ndidzamuyankha malinga ndi kuchuluka kwa mafano ake onyansa.+ 5 Ndidzatero kuti ndichititse mantha mitima ya anthu a nyumba ya Isiraeli,+ pakuti onsewo achoka kwa ine chifukwa cha mafano awo onyansa.”’+

6 “Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Bwererani, siyani mafano anu onyansa.+ Tembenuzani nkhope zanu kuti musayang’anenso zinthu zanu zonse zonyansa.+ 7 Pakuti munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo amene akukhala mu Isiraeli, amene wasiya kunditsatira+ n’kuika mtima wake pamafano ake onyansa, ndiponso amene waika pamaso pake chinthu chopunthwitsa chimene chimamulakwitsa n’kupita kwa mneneri kuti akafunsire kwa ine,+ ine Yehova ndidzamuyankha ndekha. 8 Ine ndidzamuyang’ana mokwiya+ n’kumuika kuti akhale chenjezo+ ndi mwambi.+ Ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu anga,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’+

9 “‘Ngati mneneri wapusitsidwa n’kulankhula mawu, ineyo Yehova ndi amene ndamupusitsa mneneriyo.+ Ndidzamutambasulira dzanja langa n’kumuwononga pakati pa anthu anga, Aisiraeli.+ 10 Iwo adzakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo.+ Zolakwa za wofunsira zidzakhala chimodzimodzi ndi zolakwa za mneneri,+ 11 kuti a nyumba ya Isiraeli asadzasiyenso kunditsatira n’kumangoyenda uku ndi uku,+ ndiponso kuti asadzadziipitsenso ndi zochimwa zawo zonse. Chotero iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+

12 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko landichimwira pochita zosakhulupirika,+ ndidzalitambasulira dzanja langa n’kuthyola ndodo zake zimene amakolowekapo mikate yoboola pakati.+ Komanso ndidzalitumizira njala+ ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto m’dzikolo.”+ 14 “‘Amuna atatu awa: Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu,+ akanakhala m’dzikolo, iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+

15 “‘Nditati ndichititse zilombo zolusa zakutchire kudutsa m’dzikolo,+ zilombozo n’kuliphera ana dzikolo,+ moti dzikolo n’kukhala bwinja lokhalokha popanda munthu aliyense wodutsamo chifukwa cha zilombo zolusazo,+ 16 ngakhale zikanakhala kuti amuna atatu amenewa anali kukhala m’dzikolo, pali ine Mulungu wamoyo, iwo sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena aakazi. Iwo okhawo ndiwo akanapulumutsidwa, koma dzikolo likanakhala bwinja lokhalokha,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

17 “‘Kapena nditati ndibweretse lupanga m’dzikolo,+ n’kunena kuti: “M’dzikolo mudutse lupanga,” ine n’kuphamo anthu ndi ziweto,+ 18 ngakhale amuna atatu amenewa akanakhalamo,+ pali ine Mulungu wamoyo, sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena ana awo aakazi, koma iwo okhawo ndiwo akanapulumutsidwa,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

19 “‘Kapenanso nditati nditumize mliri m’dzikolo,+ n’kukhuthulira mkwiyo wanga padzikolo, n’kukhetsa magazi+ ambiri popha anthu ndi ziweto m’dzikolo, 20 ngakhale Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu+ akanakhala m’dzikolo,+ pali ine Mulungu wamoyo, sakanapulumutsamo mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi. Iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+

21 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Zidzateronso ndikadzabweretsa ziweruzo zanga zinayi izi zowononga:+ lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri.+ Ndidzatumiza zimenezi mu Yerusalemu kuti zikaphemo anthu ndi ziweto.+ 22 Koma ndithu m’dzikolo mudzatsala kagulu ka anthu amene adzapulumuke ndipo adzatulutsidwamo.+ Taonani ana aamuna ndi aakazi! Iwo akubwera kwa inu, ndipo mudzaona njira yawo ndi zochita zawo.+ Inu mudzatonthozedwa pambuyo pa tsoka limene ndidzabweretse pa Yerusalemu, ngakhalenso pambuyo pa zonse zimene ndidzabweretsere mzindawo.’”

23 “‘Ndithu iwo adzakutonthozani mukadzaona njira zawo ndi zochita zawo. Chotero mudzadziwa kuti zonse zimene ndidzachitire mzindawo, sindinazichite popanda chifukwa,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+

15 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wa mpesa+ umasiyana bwanji ndi mitengo ina yonse? Kodi kamtengo kophuka pambali pa mtengowo pakati pa mitengo ya m’nkhalango kamasiyana bwanji ndi mitengo ina? 3 Kodi anthu amadula nthambi yake kuti ikhale mtengo wogwiritsira ntchito inayake? Kapena kodi amatengapo kamtengo koti akhome pakhoma kuti azikolowekapo ziwiya zosiyanasiyana? 4 Mtengowotu umangoikidwa pamoto basi kuti ukhale nkhuni.+ Motowo umanyeketsa kutsinde ndi kunsonga kwake. Pakati pa mtengowo pamapsanso.+ Choncho kodi mtengowo ungagwire ntchito ina iliyonse? 5 Mtengowo ukakhala wathunthu saugwiritsa ntchito iliyonse. Ndiye kuli bwanji ukapsa ndi moto n’kunyeka? Kodi ungagwirenso ntchito iliyonse?”+

6 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Mofanana ndi mtengo wa mpesa umene uli pakati pa nkhalango, umene ndaupereka kuti uzikhala nkhuni pamoto, ndaperekanso anthu okhala mu Yerusalemu.+ 7 Anthuwo ndawayang’ana mokwiya.+ Iwo achoka pamoto, koma motowo uwanyeketsa.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzawayang’ana mokwiya.’”+

8 “‘Dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja lokhalokha+ chifukwa chakuti iwo achita zosakhulupirika,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

16 Yehova analankhula nanenso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza+ Yerusalemu za zinthu zake zonyansa.+ 3 Umuuze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akunena kwa iwe Yerusalemu kuti: “Iwe unachokera kudziko la Akanani ndipo unabadwira komweko.+ Bambo ako anali Muamori,+ mayi ako anali Mhiti.+ 4 Pa tsiku limene unabadwa,+ chingwe chako cha pamchombo sichinadulidwe. Sanakusambitse kuti uyere, sanakupake mchere ndiponso sanakukulunge munsalu. 5 Palibe diso limene linakumvera chisoni kuti likuchitire chimodzi mwa zinthu zimenezi chifukwa chochita nawe chifundo.+ Koma tsiku limene unabadwa, unaponyedwa pansi chifukwa anthu ananyansidwa nawe.

6 “‘“Kenako ine ndinadutsa pafupi nawe ndipo ndinakuona ukuponyaponya timiyendo tako m’mwamba uli m’magazi ako. Ndiyeno ndinakuuza uli m’magazi akowo kuti, ‘Khalabe ndi moyo!’+ Ndithu ndinakuuza uli m’magazi akowo kuti, ‘Khalabe ndi moyo!’ 7 Ndinakusandutsa khamu lalikulu ngati udzu wophuka m’munda kuti ukule ndi kutalika,+ ndiponso kuti uvale zodzikongoletsera zabwino kwambiri.+ Mabere ako awiri anakula bwino ndipo tsitsi lako linakula kwambiri udakali wosavala ndiponso wamaliseche.”’

8 “‘Ndinadutsa pafupi nawe n’kukuona, ndipo ndinaona kuti inali nthawi yako yoti uchite zachikondi.+ Chotero ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinakulumbirira n’kuchita nawe pangano+ ndipo unakhala wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 9 ‘Komanso ndinakusambitsa.+ Ndinatsuka magazi ako n’kukudzoza mafuta.+ 10 Kenako ndinakuveka chovala cha nsalu yopeta+ ndi nsapato za chikopa cha katumbu.*+ Ndinakukulunga munsalu zabwino kwambiri+ n’kukufunditsa nsalu zamtengo wapatali. 11 Ndinakuvekanso zokongoletsera ndi zibangili+ m’manja mwako ndipo ndinakuveka mkanda+ m’khosi mwako. 12 Ndinakuveka ndolo ya pamphuno+ ndi ndolo za m’makutu*+ ndiponso chisoti chokongola pamutu pako.+ 13 Unali kuvala zinthu zagolide ndi zasiliva ndiponso nsalu zabwino kwambiri. Unali kuvala nsalu zamtengo wapatali ndi chovala cha nsalu yopeta.+ Unkadya ufa wosalala, uchi, ndi mafuta+ ndipo unakhala chiphadzuwa. Patapita nthawi unakhala woyenera ufumu.’”+

14 “‘Dzina lako linatchuka pakati pa mitundu ya anthu chifukwa cha kukongola kwako, pakuti linali labwino kwambiri chifukwa cha ulemerero wanga umene ndinaika pa iwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

15 “‘Koma unayamba kudalira kukongola kwako+ ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwa dzina lako.+ Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa m’njira.+ Kukongola kwako unakupereka kwa anthu odutsawo. 16 Unatenga zovala zako zina n’kupangira malo okwezeka+ okhala ndi mitundu yosiyanasiyana ndipo unayamba kuchitirapo uhule.+ Zoterezi siziyenera kuchitika. Zisamachitike ayi. 17 Unali kutenga zinthu zako zokongola zochokera pagolide ndi siliva wanga amene ndinakupatsa+ n’kupangira zifaniziro za munthu wamwamuna+ n’kumachita nazo uhule.+ 18 Unali kutenganso zovala zako za nsalu yopeta n’kuphimbira zifanizirozo. Komanso unkaika mafuta anga ndi zonunkhiritsa zanga+ pamaso pa zifanizirozo. 19 Ndinakupatsa chakudya choti uzidya. Ndinakupatsa ufa wosalala, mafuta, ndi uchi.+ Koma zinthu zimenezi, iwe unaziika pamaso pa zifanizirozo kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi,+ ndipo unapitiriza kuchita zimenezi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

20 “‘Unali kutenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ n’kumawapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire? 21 Iwe unali kupha ana anga,+ ndipo unali kuwapereka nsembe kwa mafano mwa kuwaponya pamoto.+ 22 M’zonyansa zako zonse ndi m’zochita zako zauhule sunakumbukire masiku a ubwana wako pamene unali wosavala ndi wamaliseche, pamene unali kuponyaponya timiyendo tako m’mwamba uli m’magazi ako.+ 23 (“Tsoka, tsoka kwa iwe,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.) Ndiyeno pambuyo pa zoipa zako zonse, 24 unadziunjikira mulu wa dothi ndipo unadzikonzera malo okwera m’bwalo lililonse la mzinda.+ 25 Unamanga malo ako okwerawo pamphambano iliyonse ya msewu+ ndipo unaipitsa kukongola kwako.+ Unayamba kukhanyulira munthu aliyense wodutsa+ n’kumachulukitsa zochita zako zauhule.+ 26 Unayamba kuchita uhule ndi ana aamuna a Iguputo,+ anthu a ziwalo zikuluzikulu amene ukukhala nawo pafupi.+ Unapitiriza kuwonjezera uhule wako kuti undikwiyitse. 27 Tsopano ine ndidzakutambasulira dzanja langa+ ndipo ndidzakuchepetsera gawo lako.+ Ndidzakupereka ku zilakolako+ za akazi odana nawe,+ ana aakazi a Afilisiti,+ akazi amene akuchita manyazi ndi khalidwe lako lotayirira.+

28 “‘Unachitanso uhule ndi ana aamuna a Asuri chifukwa chakuti sunali kukhutira.+ Unapitiriza kuchita nawo uhule koma sunakhutirebe. 29 Unawonjezera kuchita zauhule ndi dziko la Kanani+ ndiponso Akasidi.+ Ngakhale amenewanso sunakhutiritsidwe nawo. 30 Tsopano iweyo wandikwiyitsa koopsa+ chifukwa cha zonse zimene wakhala ukuchitazi. Wakhala ukuchita ntchito za hule+ lopanda m’manyazi omwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 31 ‘Ngakhale kuti unaunjika mulu wako wadothi pamphambano m’misewu, komanso unapanga malo okwera m’bwalo lililonse la mzinda, unakhala wosiyana ndi hule chifukwa sunkafuna kulipidwa. 32 Mkazi amene amachita chigololo amatenga amuna achilendo m’malo mwa mwamuna wake.+ 33 Nthawi zambiri anthu amapatsa mahule mphatso,+ koma iweyo umapereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse.+ Umawapatsa chiphuphu kuti abwere kwa iwe kuchokera kumalo onse ozungulira kuti adzachite nawe zauhule.+ 34 Iweyo umachita zosiyana ndi akazi ena pa uhule wako, ndipo palibenso amene amachita uhule wofanana ndi wako, womapereka malipiro pamene iweyo sunalipidwe. Choncho iwe ukuchita zosiyana ndi anzako.’

35 “Chotero hule iwe,+ imva mawu a Yehova.+ 36 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza wasonyeza chilakolako chako chonyansa mopitirira muyezo+ ndipo maliseche ako+ aonekera pamtunda pamene unali kuchita zauhule ndi zibwenzi zako+ ndi mafano ako onse onyansa,+ ndiponso chifukwa cha magazi a ana ako amene unawapereka kwa mafanowo,+ 37 ine ndisonkhanitsa pamodzi zibwenzi zako zonse zimene unali kuzisangalatsa. Ndisonkhanitsanso anthu onse ochokera kumalo onse okuzungulira amene unali kuwakonda limodzi ndi onse amene unali kudana nawo kuti akuukire. Ndidzakuvula pamaso pawo ndipo iwo adzaona maliseche ako onse.+

38 “‘Ndidzakupatsa chiweruzo chimene chimaperekedwa kwa akazi achigololo+ ndi kwa akazi okhetsa magazi,+ ndipo ndidzakupatsa magazi a mkwiyo ndi nsanje.+ 39 Ndidzakupereka m’manja mwa anthu okuukira ndipo iwo adzafafaniza mulu wako wadothi+ ndi malo ako okwera.+ Iwo adzakuvula zovala+ ndipo adzatenga zinthu zako zokongola+ n’kukusiya wosavala ndi wamaliseche. 40 Adzakubweretsera chigulu cha anthu+ n’kukuponya miyala+ ndipo adzakupha ndi malupanga awo.+ 41 Iwo adzatentha nyumba zako ndi moto+ ndipo adzakulanga pamaso pa akazi ambiri.+ Ine ndidzakusiyitsa uhule+ moti sudzaperekanso malipiro. 42 Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pa iwe,+ moti sindidzakuchitiranso nsanje.+ Ndidzangokhala osachita kalikonse ndipo sindidzakhalanso wokwiya.’

43 “‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako+ ndipo unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi,+ ineyo ndidzakubwezera malinga ndi zochita zako.+ Sudzachitanso khalidwe lako lotayirira komanso zinthu zako zonse zonyansa,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

44 “‘Aliyense wokunenera mwambi+ adzanena mwambi wakuti, “Make mbuu, mwana mbuu!”+ 45 Iwe ndiwe mwana wamkazi wa mayi ako,+ omwe amanyansidwa ndi mwamuna wawo+ ndi ana awo aamuna. Ndiwe m’bale wawo wa abale ako, amene amanyansidwa ndi amuna awo ndi ana awo aamuna. Akazi inu, mayi wanu anali Mhiti,+ ndipo bambo wanu anali Muamori.’”+

46 “‘Mkulu wako amene akukhala kumanzere kwako ndiye Samariya+ ndi midzi yake yozungulira.+ Mng’ono wako, amene akukhala mbali ya kudzanja lako lamanja ndi Sodomu+ ndi midzi yake yozungulira.+ 47 Iwe sikuti unangoyenda chabe m’njira zawo ndiponso sikuti unangochita zinthu motsatira zinthu zawo zonyansa,+ koma m’nthawi yochepa unayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri kuposa iwowo m’njira zako zonse.+ 48 Pali ine Mulungu wamoyo, m’bale wako Sodomu ndi midzi yake yozungulira, sanachite mofanana ndi zimene iwe ndi midzi yako yozungulira munachita,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 49 ‘Tamvera! Cholakwa cha m’bale wako Sodomu chinali, kunyada,+ kukhala ndi chakudya chokwanira+ ndiponso kukhala ndi moyo wabata+ ndi wosatekeseka. Izi n’zimene iye ndi midzi yake yozungulira anali nazo.+ Sanalimbitse dzanja la munthu wosautsika+ ndi wosauka.+ 50 Iwo anapitiriza kudzikweza+ ndi kuchita chinthu chonyansa pamaso panga+ ndipo pamapeto pake ndinawachotsa nditaona kuti n’koyenera kutero.+

51 “‘Komanso, Samariya+ sanachite machimo ofika ngakhale hafu ya machimo ako. Koma iwe unapitiriza kuchulukitsa zinthu zako zonyansa kuposa abale ako, moti unachititsa kuti iwo aoneke ngati olungama chifukwa cha zinthu zako zonse zonyansa zimene unali kuchita.+ 52 Iweyo udzachita manyazi kwambiri ukamadzaikira kumbuyo abale ako. Iwowo ndi olungama kuposa iweyo chifukwa machimo amene unachita ndi onyansa kwambiri kuposa amene iwowo anachita.+ Chotero iweyo uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa chakuti wachititsa kuti abale ako aoneke ngati olungama.’

53 “‘Ine ndidzasonkhanitsa anthu awo amene anawagwira ndi kupita nawo kudziko lina.+ Ndidzasonkhanitsa anthu ogwidwa a ku Sodomu ndi midzi yake yozungulira, ndi ogwidwa a ku Samariya ndi midzi yake yozungulira. Ndidzasonkhanitsanso anthu ako amene anagwidwa omwe ali pakati pawo,+ 54 kuti udzachite manyazi.+ Iwe udzachita manyazi chifukwa cha zonse zimene unachita pakuti unawatonthoza.+ 55 Abale akowo, Sodomu ndi midzi yake yozungulira, Samariya ndi midzi yake yozungulira, adzakhalanso monga mmene analili kale, komanso iweyo ndi midzi yako yozungulira mudzakhalanso ngati mmene munalili kale.+ 56 M’bale wako Sodomu sanali woti n’kumveka ukumutchula ndi pakamwa pako m’masiku amene iwe unali kunyada.+ 57 Zoipa zako zisanaonekere,+ Sodomu sanali woti n’kumveka ukumutchula ngati mmene zinalili pa nthawi imene ana aakazi a Siriya+ ndi onse omuzungulira, komanso ana aakazi a Afilisiti,+ anali kukunyoza kuchokera kumbali zonse.+ 58 Chotero iweyo udzakumana ndi zotsatira za khalidwe lako lotayirira+ ndiponso zotsatira za zinthu zako zonyansa,’+ watero Yehova.”

59 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Inenso ndidzakubwezera mogwirizana ndi zochita zako,+ chifukwa unanyoza lumbiro pophwanya pangano langa.+ 60 Ndithu ine ndidzakumbukira pangano limene ndinapangana ndi iwe m’masiku a ubwana wako,+ ndipo ndidzakukhazikitsira pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.*+ 61 Ndithu udzakumbukira njira zako+ ndipo udzachita manyazi ukadzalandira akulu ako ndi ang’ono ako. Ndidzawapereka kwa iwe ngati ana ako aakazi,+ koma osati chifukwa cha pangano limene ndinapangana nawe.’+

62 “‘Ineyo ndidzapangana nawe pangano+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova. 63 Ndidzachita izi kuti ndikadzakuperekera nsembe yophimba machimo+ chifukwa cha zonse zimene wachita, udzakumbukire ndi kuchita manyazi+ ndiponso kuti usadzakhale ndi chifukwa chilichonse chotsegulira pakamwa pako+ chifukwa cha manyazi ako,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

17 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, phera nyumba ya Isiraeli mwambi+ ndipo uwauze mawu ophiphiritsa.+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ku Lebanoni+ kunabwera chiwombankhanga chachikulu+ chokhala ndi mapiko aakulu+ ndi aatali. Chiwombankhangacho chinali ndi nthenga zambiri zamitundu yosiyanasiyana. Chitafika kumeneko, chinathyola nsonga ya mtengo+ wa mkungudza.+ 4 Chiwombankhangacho chinathyola nsonga yapamwamba penipeni pa nthambi zanthete, n’kupita nayo kudziko la Kanani.+ Kumeneko chinakabzala nsonga ya mkungudzayo mumzinda wa anthu ochita malonda. 5 Kenako chinatenga zina mwa mbewu za m’dzikomo+ ndi kuzibzala m’munda wolimidwa bwino. Chinabzala nsonga ya mkungudza ija ngati mtengo wa msondodzi umene uli m’mphepete mwa madzi ambiri.+ 6 Nsonga ya mkungudza ija inayamba kuphuka n’kukhala mtengo wa mpesa waufupi+ wamasamba ambiri. Nthambi za mtengowo sizinali kukulira m’mbali ndipo unaphuka mizu pansi pake. Pomalizira pake nsongayo inakhala mtengo wa mpesa ndipo inaphuka ndi kuchita nthambi.+

7 “‘“Kenako kunabwera chiwombankhanga china chachikulu+ chokhala ndi mapiko aakulu anthenga zikuluzikulu.+ Ndiyeno mwanjala, mtengo wa mpesawo unatambasula mizu yake ndi nthambi zake kuchokera pamene unabzalidwa kukafika pamene panali chiwombankhangacho+ kuti chithirire mtengowo.+ 8 Koma mtengowo anali ataubzala m’munda wabwino, m’mphepete mwa madzi ambiri,+ kuti uchite nthambi ndi kubereka zipatso n’kukhala mtengo waukulu wa mpesa.”’

9 “Ndiyeno unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mtengo umenewu zinthu zidzauyendera bwino?+ Kodi munthu wina sadzadula mizu yake+ ndi kuwononga zipatso zake? Kodi mphukira zake zimene zangothyoledwa kumene sizidzauma?+ Mtengowo udzauma ndithu. Sudzachita kufuna dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti uzulidwe ndi mizu yomwe. 10 Ngakhale kuti mtengowo anautenga pamalo ena n’kukaubzala pamalo ena, kodi zinthu zidzauyendera bwino? Kodi sudzaumiratu ukadzawombedwa ndi mphepo ya kum’mawa?+ Udzauma ndithu pamalo amene unabzalidwapo.”’”+

11 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 12 “Chonde, uza nyumba yopandukayi+ kuti, ‘Kodi anthu inu simukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Auze kuti, ‘Mfumu ya Babulo inabwera ku Yerusalemu n’kudzatenga mfumu+ ndi akalonga a mumzindawo ndi kupita nawo ku Babulo.+ 13 Kuwonjezera apo, inatenga mmodzi wa mbewu yachifumu+ n’kuchita naye pangano ndi kumulumbiritsa.+ Mfumuyo inatenga atsogoleri a m’dzikolo n’kupita nawo kwawo,+ 14 kuti ufumuwo ukhale waung’ono, usakule,+ komanso kuti ukhalepobe mwa kusunga pangano limene anachita.+ 15 Koma iye anapandukira+ mfumuyo potumiza amithenga ku Iguputo kuti dziko la Iguputo limupatse mahatchi*+ ndi khamu la anthu. Kodi zinthu zidzamuyendera bwino? Kodi munthu amene akuchita zinthu zimenezi ndiponso amene akuphwanya pangano adzapulumuka? Kodi iye adzapulumukadi?’+

16 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo,+ munthu amene ananyoza lumbiro+ ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu imene inamulonga ufumu, adzafera m’dziko la mfumu yomweyo, dziko la Babulo.+ 17 Farao sadzamutumizira gulu lalikulu la asilikali ndi khamu la anthu kuti amuthandize pankhondo.+ Sadzamuthandiza mwa kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo n’cholinga chakuti aphe anthu ambiri.+ 18 Ngakhale kuti anatambasula dzanja lake+ povomereza lumbiro, iye wanyoza lumbiro+ limenelo mwa kuphwanya pangano. Iye wachita zinthu zonsezi ndipo sadzapulumuka.”’+

19 “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzamulanga ndithu chifukwa cha lumbiro langa limene walinyoza+ ndiponso pangano langa limene waliphwanya. 20 Ndidzam’ponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo ndi kumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+ 21 Gulu lonse la asilikali ake amene anathawa, lidzaphedwa ndi lupanga. Amene adzapulumuke adzabalalikira ku mphepo zonse.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine Yehova ndi amene ndanena zimenezi.”’+

22 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inenso ndidzathyola nsonga ya pamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza.+ Ndidzabudula nsonga yanthete kunthambi zake+ ndipo ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali.+ 23 Ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali la ku Isiraeli+ ndipo idzachita nthambi ndi kubereka zipatso+ n’kukhala mtengo waukulu wa mkungudza.+ Mbalame zamitundu yonse zizidzakhala pansi pa mtengowo ndi mumthunzi wa masamba ake.+ 24 Mitengo yonse yamthengo idzadziwa kuti ine Yehova+ ndatsitsa mtengo waukulu+ ndi kukweza mtengo wonyozeka,+ ndaumitsa mtengo wauwisi+ ndi kuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma. Ine Yehova ndanena ndi kuchita zimenezi.”’”+

18 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Kodi mukutanthauza chiyani mukamanena mwambi m’dziko la Isiraeli wakuti, ‘Bambo ndi amene amadya mphesa zosapsa koma mano a ana awo ndiwo amayayamira’?+

3 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, simudzanenanso mwambi umenewu mu Isiraeli. 4 Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga.+ Moyo+ wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga.+ Moyo umene ukuchimwawo+ ndi umene udzafe.+

5 “‘Munthu akakhala wolungama n’kumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ 6 ngati sadya+ zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri,+ ngati sakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli,+ ngati saipitsa mkazi wa mnzake,+ ngati sayandikira mkazi amene wadetsedwa,+ 7 ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+ 8 ngati salandira chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu,+ ndiponso sakongoza zinthu mwa katapira,*+ ngati sachita zopanda chilungamo,+ ngati amachita chilungamo chenicheni poweruza munthu ndi mnzake,+ 9 ngati akuyendabe m’malamulo anga+ ndi kusunga zigamulo zanga kuti azichita mogwirizana ndi choonadi,+ ndiye kuti munthu wotero ndi wolungama.+ Ndithu adzakhalabe ndi moyo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

10 “‘Munthu akabereka mwana wamwamuna, mwanayo n’kukhala wakuba,+ wokhetsa magazi,+ ndipo amachita chilichonse cha zinthu zimenezi, 11 (koma bamboyo sanachitepo chilichonse mwa zinthu zimenezi), ngati mwanayo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri+ ndipo amaipitsa mkazi wa mnzake,+ 12 ngati amazunza munthu wosautsika ndi wosauka,+ ngati amalanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati sabweza chikole,+ ngati amakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa,+ ndiye kuti wachita chinthu chonyansa.+ 13 Iye amakongoza zinthu zake mwa katapira+ ndipo amalandira chiwongoladzanja.+ Ndithudi iye sadzakhala ndi moyo chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi.+ Adzaphedwa ndithu, ndipo magazi ake adzakhala pamutu pake.+

14 “‘Ndiyeno munthu wina wabereka mwana wamwamuna amene amaona machimo onse amene bambo ake amachita. Mwanayo amaona machimowo koma sawachita.+ 15 Iye sadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri. Sakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli+ ndipo sanaipitsepo mkazi wa mnzake.+ 16 Sanazunzepo munthu aliyense.+ Sanatengepo chikole+ ndipo sanalandepo chilichonse mwauchifwamba.+ Munthu wanjala amam’patsa chakudya+ ndipo munthu wamaliseche amam’phimba ndi chovala.+ 17 Iye sapondereza munthu wosautsika. Sakongoza zinthu mwa katapira+ ndipo salandira chiwongoladzanja.+ Amatsatira zigamulo zanga+ ndi kuyenda motsatira malamulo anga.+ Munthu wotere sadzafa chifukwa cha zolakwa za bambo ake.+ Adzakhalabe ndi moyo.+ 18 Koma bambo akewo, adzafa chifukwa cha zolakwa zawo,+ popeza anabera anthu mwachinyengo,+ anabera m’bale wawo zinthu mwauchifwamba+ ndipo anachita choipa chilichonse pakati pa anthu a mtundu wawo.+

19 “‘Anthu inu mudzanena kuti: “N’chifukwa chiyani mwanayo alibe mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake?”+ Mwanayo anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo.+ Iye anasunga malamulo anga ndipo akupitiriza kuwatsatira.+ Ndithudi adzakhalabe ndi moyo.+ 20 Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake. Bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake.+ Chilungamo cha munthu wolungama chidzakhala pa iye,+ ndipo zoipa za munthu woipa zidzakhala pamutu pa woipayo.+

21 “‘Munthu woipa akabwerera, kusiya machimo ake onse amene anali kuchita+ ndipo akasunga malamulo anga onse n’kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ adzakhalabe ndi moyo. Sadzafa ayi.+ 22 Zolakwa zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo.+ Adzakhalabe ndi moyo chifukwa cha zinthu zolungama zimene anachita.’+

23 “‘Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu aliyense wochimwa?+ Kodi sindisangalala kuti munthu wochimwayo abwerere kusiya njira zakezo ndi kukhalabe ndi moyo?’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

24 “‘Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo,+ akamachita zopanda chilungamo+ n’kumakhalabe ndi moyo, zinthu zolungama zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa.+ Iye adzafa chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika ndiponso chifukwa cha machimo ake amene anachita.+

25 “‘Anthu inu mudzanena kuti: “Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.”+ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo?+ Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?+

26 “‘Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo+ n’kufa chifukwa cha zochita zakezo, wafa chifukwa cha zochita zake zopanda chilungamo.+

27 “‘Munthu woipa akasiya zinthu zoipa zimene anali kuchita n’kumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ iyeyu adzapulumutsa moyo wake.+ 28 Munthu woipayo akaona+ zoipa zimene anali kuchita n’kuzisiya,+ adzakhalabe ndi moyo. Sadzafa ayi.+

29 “‘Ndithu nyumba ya Isiraeli idzanena kuti: “Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.”+ Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo, inu a nyumba ya Isiraeli?+ Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?’+

30 “‘Chotero ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Lapani ndi kusiya zolakwa zanu zonse+ ndipo musalole kuti chilichonse chizikupunthwitsani ndi kukulakwitsani.+ 31 Tayani zolakwa zanu zonse zimene munachita+ ndipo muyesetse kukhala ndi mtima watsopano+ ndiponso mzimu watsopano.+ Kodi muferenji+ inu a nyumba ya Isiraeli?’

32 “‘Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Choncho tembenukani anthu inu, kuti mukhale ndi moyo.’”+

19 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira+ yokhudza atsogoleri a Isiraeli.+ 2 Unene kuti, ‘Kodi mayi anu anali ndani? Anali mkango waukazi pakati pa mikango ina.+ Mkango waukaziwo unali kugona pakati pa mikango yamphamvu yamphongo, ndipo unalera ana ake.

3 “‘Patapita nthawi, mkangowo unalera mwana wake mmodzi mpaka kukula.+ Mwanayo anakhala mkango wamphamvu wamphongo. Anaphunzira kupha nyama+ ndipo anayamba kudya ngakhale anthu. 4 Mitundu ya anthu inali kumva za mkangowo. Kenako unagwera m’mbuna zawo ndipo anaukola ndi ngowe n’kupita nawo ku Iguputo.+

5 “‘Mkango waukazi uja utaona kuti wadikira popanda chilichonse chochitika, ndipo palibenso chiyembekezo chilichonse, unatenganso mwana wake wina.+ Unalera mwanayo mpaka kukhala mkango wamphamvu. 6 Mkangowo unayamba kuyendayenda pakati pa mikango ina. Unakhaladi mkango wamphamvu wamphongo. Pang’onopang’ono unaphunzira kupha nyama+ ndipo unayamba kudya ngakhale anthu.+ 7 Mkango wamphongowo unadziwa nsanja zokhalamo anthu ndipo unawononga mizinda yawo.+ Chotero dzikolo linakhala bwinja moti munkangomveka kubangula kwa mkangowo.+ 8 Mitundu ya anthu a m’zigawo zonse zozungulira anabwera kudzauukira.+ Anauponyera ukonde+ wawo ndipo mkangowo unagwera m’mbuna zawo.+ 9 Kenako anaukola ndi ngowe n’kuuika m’kakhola ndi kupita nawo kwa mfumu ya Babulo.+ Anapita nawo ataukulunga ndi ukonde wosakira kuti mawu ake asamvekenso m’mapiri a ku Isiraeli.+

10 “‘Mayi anu+ anali ngati mtengo wa mpesa*+ wobzalidwa m’mphepete mwa madzi. Mtengowo unali kubereka zipatso ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa unali pamadzi ambiri.+ 11 Nthambi za mtengowo zinakhala zolimba zoyenera kupangira ndodo zachifumu za olamulira.+ Patapita nthawi, mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo ina, ndipo unali kuonekera patali chifukwa cha kutalika kwake ndi kuchuluka kwa masamba ake.+ 12 Koma pamapeto pake, mtengowo unazulidwa ndi manja aukali+ n’kuponyedwa pansi. Kenako kunabwera mphepo ya kum’mawa n’kuumitsa zipatso zake.+ Ndodo yake yolimba inathyoledwa n’kuuma+ ndipo inanyeka ndi moto.+ 13 Tsopano mtengo wa mpesawo wabzalidwa m’chipululu,+ m’dziko lopanda madzi ndi louma.+ 14 Kenako moto unatuluka m’ndodo yake+ n’kunyeketsa nthambi zake ndi zipatso zake, ndipo mtengowo unalibenso ndodo yolimba yachifumu.+

“‘Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’”+

20 M’chaka cha 7, m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine kudzafunsira kwa Yehova,+ ndipo anakhala pamaso panga.+ 2 Ndiyeno Yehova analankhula nane kuti: 3 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi amuna inu mwabweradi kudzafunsira kwa ine?+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti inu mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’

4 “Kodi ndiwe wokonzeka kuwaweruza? Kodi uwaweruza, iwe mwana wa munthu?+ Auze zinthu zonyansa zimene makolo awo anachita.+ 5 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli,+ ndinakweza mkono wanga+ polumbirira mbewu ya nyumba ya Yakobo+ ndi kuwachititsa kuti andidziwe m’dziko la Iguputo.+ Inde, ndinakweza mkono wanga ndi kuwalumbirira kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+ 6 Pa tsiku limenelo ndinakweza dzanja langa+ powalumbirira kuti ndidzawatulutsa m’dziko la Iguputo kupita nawo kudziko limene ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Linali dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse.+ 7 Ine ndinawauza kuti, ‘Aliyense wa inu ataye zinthu zake zonyansa zimene amaziyang’anitsitsa pozilambira+ ndipo musadziipitse ndi mafano onyansa a ku Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+

8 “‘“Koma iwo anayamba kundipandukira+ ndipo sanafune kundimvera. Aliyense wa iwo sanataye zinthu zonyansa zimene anali kuziyang’anitsitsa pozilambira ndipo sanasiye mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga kuti ukali wanga uthere pa iwo m’dziko la Iguputo.+ 9 Koma ine ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene iwo anali kukhala pakati pawo,+ pakuti ndinawachititsa kuti andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo powatulutsa m’dziko la Iguputo.+ 10 Chotero ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo ndi kuwalowetsa m’chipululu.+

11 “‘“Kumeneko ndinawapatsa malamulo+ ndi kuwadziwitsa zigamulo zanga,+ kuti munthu amene akuzitsatira akhalebe ndi moyo.+ 12 Ndinawapatsanso sabata langa+ kuti likhale chizindikiro pakati pa ine ndi iwowo.+ Ndinachita zimenezi n’cholinga choti adziwe kuti ine Yehova, ndiye amene ndikuwapatula.

13 “‘“Koma iwowo, a nyumba ya Isiraeli, anandipandukira m’chipululu.+ Iwo sanayende motsatira malamulo anga+ ndipo anakana zigamulo zanga+ zimene munthu akamazitsatira, amakhala ndi moyo.+ Sabata langa analidetsa kwambiri,+ moti ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga m’chipululu kuti ndiwafafanize.+ 14 Koma ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 15 Ine ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu+ kuti sindidzawalowetsa m’dziko limene ndinawapatsa, dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ (dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse)+ 16 chifukwa anakana zigamulo zanga, sanayende motsatira malamulo anga, anadetsa sabata langa komanso mtima wawo unali pa mafano awo onyansa.+

17 “‘“Maso anga anayamba kuwamvera chisoni kuti ndisawawononge,+ chotero sindinawafafanize m’chipululu. 18 Choncho ndinauza ana awo m’chipululu kuti,+ ‘Musayende motsatira malamulo a makolo anu,+ ndipo musasunge zigamulo zawo.+ Musadziipitse ndi mafano awo onyansa.+ 19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Yendani motsatira malamulo anga+ ndipo musunge zigamulo zanga+ ndi kuzitsatira.+ 20 Muzisunga sabata langa kuti likhale lopatulika+ ndipo likhale chizindikiro pakati pa ine ndi inu, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+

21 “‘“Koma anawo anayamba kundipandukira.+ Sanayende motsatira malamulo anga ndipo sanasunge ndi kutsatira zigamulo zanga, zimene ngati munthu atazitsatira angakhale ndi moyo.+ Iwo anadetsa sabata langa,+ choncho ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga, kuti ukali wanga uthere pa iwo m’chipululu.+ 22 Ine ndinabweza dzanja langa+ ndi kuchita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 23 Komanso ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu,+ kuti ndidzawabalalitsira ku mitundu ya anthu ndi kuwamwazira m’mayiko osiyanasiyana,+ 24 chifukwa chakuti sanatsatire zigamulo zanga,+ anakana malamulo anga,+ anadetsa sabata langa+ komanso maso awo anali pa mafano onyansa a makolo awo.+ 25 Chifukwa cha zimenezi ine ndinawalola kutsatira malamulo oipa ndi zigamulo zimene sizikanawathandiza kukhala ndi moyo.+ 26 Ndinawalola kudziipitsa ndi mphatso zawo pamene anali kuponya pamoto* mwana aliyense woyamba kubadwa.+ Ndinachita zimenezi kuti ndiwasautse n’cholinga choti adziwe kuti ine ndine Yehova.”’+

27 “Choncho iwe mwana wa munthu, lankhula ndi nyumba ya Isiraeli ndipo uwauze kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Makolo anu anandilankhulira mawu onyoza pamene anali kundichitira zinthu mosakhulupirika.+ 28 Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko+ limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali+ ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+ 29 Choncho ndinawafunsa kuti, ‘Kodi malo okwezekawa ndi a chiyani? Kodi mumachitako chiyani kumeneko kuti malowo azitchedwa kuti Malo Okwezeka mpaka lero?’”’+

30 “Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi anthu inu mukudziipitsa potsatira njira za makolo anu?+ Kodi mukutsatira zinthu zawo zonyansa ndi kuchita zachiwerewere ndi mafano amenewo?+ 31 Kodi mukudziipitsa polemekeza mafano anu onse onyansa mpaka lero,+ popereka mphatso zanu mwa kuponya pamoto ana anu aamuna?+ Kodi pa nthawi imodzimodziyo ndilole kuti mufunsire kwa ine, inu anthu a nyumba ya Isiraeli?”’+

“‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32 ‘Ndithu zimene mukuganiza+ sizichitika.+ Inu mukunena kuti: “Tiyeni tikhale ngati anthu a mitundu ina. Tikhale ngati mabanja a m’mayiko ena+ potumikira mitengo ndi miyala.”’”+

33 “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ndidzakhala mfumu yanu ndipo ndidzakulamulirani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula+ ndi mkwiyo wosefukira.+ 34 Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumayiko amene munabalalikirako. Ndidzakusonkhanitsani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 35 Ndidzakulowetsani m’chipululu cha mitundu ya anthu+ ndipo kumeneko ndidzatsutsana nanu pamasom’pamaso.+

36 “‘Monga mmene ndinatsutsirana ndi makolo anu m’chipululu cha dziko la Iguputo,+ ndidzatsutsananso ndi inu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 37 ‘Ndidzakudutsitsani pansi pa ndodo ya m’busa+ ndi kuchita nanu pangano lolimba.+ 38 Ndidzachotsa pakati panu anthu ondipandukira ndi ondichimwira.+ Pakuti ndidzawatulutsa m’dziko limene akukhalamo monga alendo, koma sadzalowa m’dziko la Isiraeli,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

39 “Inu a nyumba ya Isiraeli, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pitani, aliyense wa inu akatumikire mafano ake onyansawo.+ Pambuyo pake, ngati simundimvera ndidzakusiyani ndipo simudzadetsanso dzina langa loyera ndi mphatso zanu ndiponso mafano anu onyansa.’+

40 “‘Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira m’phiri langa loyera,+ phiri lalitali la m’dziko la Isiraeli,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Kumeneko ndidzasangalala nawo ndipo ndidzafuna zopereka zanu ndi nsembe zanu za zinthu zoyambirira kucha pa zinthu zanu zonse zopatulika.+ 41 Ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira,+ ndidzasangalala nanu chifukwa cha nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi,+ ndipo ndidzakhala woyera chifukwa cha inu pamaso pa anthu a mitundu ina.’+

42 “‘Ndikadzakulowetsani m’dziko la Isiraeli,+ dziko limene ndinalumbira nditakweza dzanja kuti ndidzalipereka kwa makolo anu, anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 43 Ndithu kumeneko mudzakumbukira njira zanu+ ndi zochita zanu zonse zimene munali kudziipitsa nazo.+ Mukadzakumbukira zimenezi, mudzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zanu chifukwa cha zoipa zonse zimene munachita.+ 44 Ndikadzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa,+ inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine sindidzachitapo kanthu mogwirizana ndi njira zanu zoipa kapena zochita zanu zosayenera,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

45 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 46 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ ku mbali ya kum’mwera ndipo ulankhule+ mawu onena za kumeneko. Ulosere kunkhalango ya dziko la kum’mwera. 47 Uuze nkhalango ya kum’mwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa moto.+ Motowo unyeketsa mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma.+ Malawi a motowo sadzatheka kuwazimitsa,+ ndipo nkhope zonse,* kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto zidzapsa ndi moto.+ 48 Anthu onse adzaona kuti ine Yehova ndaiyatsa moto nkhalangoyo ndipo sudzatheka kuuzimitsa.”’”+

49 Ine ndinanena kuti: “Kalanga ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Iwo akundinena kuti, ‘Kodi si miyambi imene akunenayi?’”+

21 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana ku Yerusalemu ndipo ulankhule+ kwa malo oyera.+ Ulosere zoipa zimene zidzachitikire dziko la Isiraeli.+ 3 Uuze dziko la Isiraeli kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndidzakulanga.+ Ndidzasolola lupanga langa m’chimake+ ndi kupha anthu ako olungama ndiponso anthu ako oipa.+ 4 Ndidzatulutsa lupanga langa m’chimake ndi kupha anthu onse kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto. Ndidzachita izi kuti ndiphe anthu ako olungama ndiponso anthu ako oipa.+ 5 Anthu onse adzadziwa kuti ine Yehova ndasolola lupanga langa m’chimake,+ ndipo sindidzalibwezeramonso.”’+

6 “Koma iwe mwana wa munthu, buula mwamantha.+ Ubuule pamaso pawo mowawidwa mtima.+ 7 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ukubuula?’+ Uwayankhe kuti, ‘N’chifukwa cha uthenga umene ndamva.’+ Pakuti uthengawo udzafika ndithu+ ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha.+ Anthu onse adzazizira nkhongono. Aliyense adzataya mtima ndipo mawondo onse adzachucha madzi.*+ ‘Uthengawo ufika ndithu+ ndipo zimene ukunena zidzachitikadi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

8 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 9 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Nena mofuula kuti, ‘Lupanga! Lupanga!+ Lupanga lanoledwa+ ndi kupukutidwa. 10 Lupanga lanoledwa pokonzekera kupha anthu. Lapukutidwa kuti linyezimire.’”’”+

“Koma kodi tilibe chifukwa chosangalalira?”+

“‘Kodi lupangalo likukana ndodo yachifumu+ ya mwana wanga,+ ngati mmene likukanira mtengo uliwonse?+

11 “‘Wina wapereka lupangalo kuti lipukutidwe n’cholinga choti alinyamule ndi kuligwiritsa ntchito. Lupangalo lanoledwa ndi kupukutidwa kuti alipereke m’dzanja la munthu wakupha.+

12 “‘Lira ndi kufuula+ iwe mwana wa munthu, chifukwa lupangalo laukira anthu anga.+ Laukira atsogoleri onse a Isiraeli.+ Atsogoleriwo aperekedwa kuti aphedwe ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga.+ Chotero menya pantchafu yako chifukwa cha chisoni.+ 13 Lupangalo layesedwa kuti aone ngati lili lakuthwa.+ Kodi chidzachitike n’chiyani ngati lupangalo likukana ndodo yachifumu?+ Ndodoyo sidzapitiriza kukhalapo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

14 “Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uwombe m’manja.+ Unene katatu mawu akuti ‘Lupanga!’+ Limeneli ndi lupanga lopha anthu. Lupanga limeneli ndi limene lapha munthu wotchuka, ndipo lazungulira anthu.+ 15 Ndidzapha anthu ndi lupanga kuti mitima ya anthu isungunuke ndi mantha,+ komanso kuti ndidzachulukitse anthu ogonjetsedwa m’zipata zawo zonse.+ Kalanga ine! Lupangalo likunyezimira. Alipukuta kuti liphe anthu.+ 16 Iwe lupanga, sonyeza kuti ndiwe wakuthwa.+ Pita mbali ya kudzanja lamanja. Sankha malo ako. Pita mbali ya kudzanja lamanzere. Pita kulikonse kumene nkhope yako yaloza. 17 Ine ndidzawomba m’manja+ chifukwa cha ukali ndipo ndidzathetsa mkwiyo wanga.+ Ine Yehova ndanena.”

18 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 19 “Koma iwe mwana wa munthu, konza misewu iwiri yoti lupanga la mfumu ya Babulo lidzadutsemo.+ Misewu yonseyo ichokere m’dziko limodzi. Pamsewu wopita mumzindawo, uikepo chikwangwani cholozera kumeneko.+ 20 Ukonze msewu woti lupanga lidzadutsemo pokaukira mzinda wa Raba+ wa ana a Amoni, ndi msewu wina woti lidzadutsemo pokaukira Yuda, inde pokaukira mzinda wa Yerusalemu wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.+ 21 Mfumu ya Babulo yaima chilili pamene panakumana misewu iwiri kuti iwombeze maula.+ Mfumuyo yagwedeza mivi, yafunsira kwa aterafi*+ ndi kuyang’ana pachiwindi cha nyama. 22 M’dzanja lake lamanja, maulawo asonyeza kuti iye apite ku Yerusalemu, kuti akaike zida zogumulira mzindawo,+ akalamule asilikali ake kuti aphe anthu, akalize chizindikiro chochenjeza,+ akaike zida zogumulira zipata za mzindawo, ndiponso kuti akamange chiunda chomenyerapo nkhondo, ndi mpanda womenyerapo nkhondo.+ 23 Kwa anthu amene anachita nawo malumbiro,+ maulawo aoneka ngati abodza.+ Mfumu ya Babuloyo yakumbukira zolakwa zawo+ kuti iwagwire ukapolo.+

24 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Anthu inu, adani anu adzakugwirani chifukwa chakuti zolakwa zanu zinaululidwa ndipo munachititsa kuti zikumbukiridwe.+ Ndithu adzakugwirani chifukwa machimo anu, kapena kuti zochita zanu zauchimo zinaonekera ndipo simunaiwalidwe.’+

25 “Koma iwe mtsogoleri+ wa Isiraeli, woipa ndi wovulazidwa koopsa,+ nthawi yafika yoti ulangidwe. Mapeto a zolakwa zako afika.+ 26 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chotsa nduwira* ndipo vula chisoti chachifumu.+ Zinthu zasintha tsopano.+ Kweza munthu wotsika+ ndipo tsitsa munthu wokwezeka.+ 27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+

28 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena zokhudza ana a Amoni ndi chitonzo chochokera kwa iwo.’ Unene kuti, ‘Lupanga lasololedwa kuti liphe anthu. Lapukutidwa kuti liwononge komanso kuti linyezimire,+ 29 chifukwa chakuti olosera anu anakuuzani masomphenya abodza,+ chifukwa chakuti anakulosererani zabodza, kuti mukhale pagulu la anthu ophedwa, anthu oipa amene tsiku lawo loti alangidwe lafika. Mapeto a zolakwa zawo zonse afika.+ 30 Bwezerani lupanga m’chimake. Ndidzakuweruzirani kwanu, m’dziko limene munachokera.+ 31 Ndidzakudzudzulani mwamphamvu. Ndidzakupemererani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo ndidzakuperekani m’manja mwa anthu osaganiza bwino, akatswiri odziwa kuwononga.+ 32 Mudzakhala ngati nkhuni pamoto.+ Magazi anu adzayenderera m’dzikolo. Inu simudzakumbukiridwanso, pakuti ine Yehova ndanena.’”+

22 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kuweruza?+ Kodi uweruza mzinda umene uli ndi mlandu wa magaziwu+ ndi kuudziwitsa zonyansa zake zonse?+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mzinda umene ukukhetsa magazi+ kufikira nthawi yako yoweruzidwa itakwana,+ iwe mzinda umene wapanga mafano onyansa kuti udzidetse nawo,+ 4 uli ndi mlandu wa magazi amene wakhetsa+ ndipo wadzidetsa chifukwa cha mafano onyansa amene wapanga.+ Wafupikitsa masiku a moyo wako ndipo zaka zoti ulandire chilango zafika. Choncho ndidzakusandutsa chinthu chotonzedwa pakati pa mitundu ina ya anthu ndiponso ndidzakusandutsa chinthu chimene mayiko onse adzachiseka ndi kuchikuwiza.+ 5 Mayiko amene uli nawo pafupi ndiponso amene ali kutali ndi iwe adzakukuwiza, iwe mzinda wa dzina lodetsedwa komanso wachisokonezo chachikulu.+ 6 Mwa iwetu muli atsogoleri+ a Isiraeli. Aliyense wa iwo akugwiritsa ntchito dzanja lake modzipereka kuti akhetse magazi.+ 7 Anthu anyoza abambo ndi amayi awo mwa iwe.+ Mlendo wokhala mwa iwe amuchitira zinthu mwachinyengo.+ Azunza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.”’”+

8 “‘Iwe wanyoza malo anga oyera, ndipo wadetsa sabata langa.+ 9 Mwa iwe muli anthu amiseche amene akukhetsa magazi.+ Iwo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri.+ Achita khalidwe lotayirira mwa iwe.+ 10 Anthu avula bambo awo.+ Iwo agona ndi mkazi wodetsedwa amene akusamba.+ 11 Munthu wachita zinthu zonyansa ndi mkazi wa mnzake,+ ndipo munthu wachita khalidwe lotayirira mwa kugona ndi mkazi wa mwana wake.+ Munthu wagona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake.+ 12 Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

13 “‘Ine ndawomba m’manja*+ chifukwa cha phindu lachinyengo limene wapeza+ komanso chifukwa cha zochita zako zokhetsa magazi zimene zili pakati pako.+ 14 Kodi mtima wako udzapitiriza kupirira,+ kapena kodi manja ako adzakhala ndi mphamvu m’masiku amene ndidzakulange?+ Ine Yehova ndanena ndipo ndidzachitapo kanthu.+ 15 Anthu ako ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndipo ndidzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+ Komanso ndidzachotsa zodetsa zako mwa iwe.+ 16 Ndithudi udzaipitsidwa pamaso pa mitundu ina, ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

17 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kwa ine a nyumba ya Isiraeli akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo.+ Onsewo ali ngati mkuwa, tini, chitsulo ndi mtovu m’ng’anjo. Iwo akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga siliva.+

19 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti nonsenu mwakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo,+ ine ndikusonkhanitsani pamodzi mu Yerusalemu.+ 20 Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amenewa ndili wokwiya ndiponso waukali. Ndidzawasonkhanitsa ngati mmene anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo,+ mtovu ndi tini m’ng’anjo kuti zinthu zimenezi azikolezere+ moto ndi kuzisungunula.+ Choncho anthu inu ndidzakukolezerani moto ndi kukusungunulani. 21 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ndi kukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22 Monga mmene anthu amasungunulira siliva m’ng’anjo, inenso ndidzakusungunulani mumzindawo. Chotero inu mudzadziwa kuti ine Yehova ndakutsanulirani mkwiyo wanga.’”+

23 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, uza dzikoli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko limene silikuyeretsedwa. Pa tsiku limene udzadzudzulidwe mwamphamvu, mwa iwe simudzagwa mvula.+ 25 Aneneri ako akukonza chiwembu mwa iwe.+ Iwo akukhadzula anthu+ ngati mkango wobangula umene wagwira nyama.+ Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali.+ Achulukitsa akazi amasiye mmenemo.+ 26 Ansembe ako aphwanya chilamulo changa modzionetsera,+ ndipo akuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa+ zinthu zoyera ndi zinthu wamba.+ Sanauze anthu kusiyana kwa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyera.+ Anyalanyaza sabata langa+ ndipo andichitira mwano pakati pawo.+ 27 Atsogoleri a mumzindawo ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi+ ndiponso kuwononga miyoyo n’cholinga chopeza phindu mwachinyengo.+ 28 Aneneri a mumzindawo apaka laimu machimo a atsogoleriwo.+ Aona masomphenya onama+ ndipo akuloserera atsogoleriwo zinthu zabodza.+ Iwo akunena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse. 29 Anthu a m’dzikolo abera anthu pochita zachinyengo+ ndiponso zauchifwamba.+ Iwo akuzunza anthu osautsika ndi osauka.+ Abera mlendo pochita zachinyengo komanso zopanda chilungamo.’+

30 “‘Ndinafunafuna munthu pakati pawo amene angathe kukonzanso mpanda wamiyala+ ndi kuima pamalo ogumuka a mpandawo+ kuti ateteze dzikolo n’cholinga choti ine ndisaliwononge,+ koma sindinapeze aliyense. 31 Choncho ndidzawadzudzula mwamphamvu.+ Ndidzawafafaniza ndi moto wa mkwiyo wanga.+ Ndidzawalanga malinga ndi zochita zawo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

23 Yehova anapitiriza kulankhula nane+ kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, panali akazi awiri, ana aakazi obadwa kwa mayi mmodzi.+ 3 Akazi amenewa anayamba kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ Anayamba uhule umenewu ali atsikana ang’onoang’ono.+ Kumeneko amuna anafinya mabere awo+ ndi kutsamira chifuwa chawo ali anamwali. 4 Wamkulu dzina lake anali Ohola, wamng’ono anali Oholiba. Akazi amenewa anakhala anga+ ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.+ Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.+

5 “Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Anali kulakalaka kwambiri amuna amene ankakhumba kugona naye.+ Anali kulakalaka Asuri+ amene anali kukhala moyandikana naye. 6 Anali kulakalaka abwanamkubwa ovala zovala zabuluu ndiponso ankalakalaka atsogoleri. Onsewa anali anyamata osiririka, asilikali okwera pamahatchi. 7 Iye anapitiriza kuchita zauhule zakezo ndi amuna onse osankhidwa a ku Asuri. Anadziipitsa ndi amuna onse amene anawakhumba ndiponso ndi mafano awo onyansa.+ 8 Iye sanasiye zauhule zake zimene anachokera nazo ku Iguputo. Aiguputowo anagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ndiwo anatsamira chifuwa chake ali namwali ndipo anali kuchita naye zachiwerewere.+ 9 Choncho ndinam’pereka m’manja mwa amuna amene anali kukhumba kugona naye.+ Ndinam’pereka m’manja mwa ana aamuna a ku Asuri amene iye anali kuwakhumba.+ 10 Amuna amenewa ndiwo amene anamuvula.+ Iwo anatenga ana ake aamuna ndi aakazi+ ndipo iyeyo anamupha ndi lupanga. Iye anatchuka ndi khalidwe loipa pakati pa akazi ena ndipo iwo anamuweruza.

11 “Mng’ono wake Oholiba ataona zimenezi,+ anayamba kukonda chiwerewere chodziwononga nacho kuposa mkulu wake. Anayamba kuchita uhule kuposa dama la mkulu wake.+ 12 Iye anali kulakalaka kwambiri ana aamuna a ku Asuri.+ Anali kulakalaka abwanamkubwa ndi atsogoleri amene anali kukhala moyandikana naye. Amuna onsewa anali ovala mwaulemerero, asilikali okwera pamahatchi komanso anyamata osiririka.+ 13 Oholiba atadziipitsa, ine ndinaona kuti akazi onsewa anali ndi khalidwe lofanana.+ 14 Iye anawonjezera zochita zake zauhule ataona zithunzi za amuna zogoba pakhoma,+ zithunzi+ za Akasidi zopaka utoto wofiira,+ 15 zithunzi za amuna ovala malamba m’chiuno,+ ndiponso ovala nduwira zazitali zolendewera kumutu kwawo. Amuna onsewo anali kuoneka ngati ankhondo, komanso ngati ana aamuna a ku Babulo, obadwira m’dziko la Kasidi. 16 Ataona zithunzizo, anayamba kukhumba kwambiri amunawo+ ndipo anatumiza anthu ku Kasidi kuti akawaitane.+ 17 Ana aamuna a ku Babulowo anali kubwera kwa iye. Anali kupita kubedi lake lochitirapo zachikondi ndi kumuipitsa ndi chiwerewere chawo.+ Iye anapitiriza kuipitsidwa ndi amunawo kenako ananyansidwa nawo n’kuwasiya.

18 “Oholiba anayamba kuchita uhule modzionetsera ndipo anali kudzivula,+ moti ine ndinasiya kukhala naye chifukwa chonyansidwa naye, monga mmene ndinasiyira mkulu wake chifukwa chonyansidwa naye.+ 19 Oholiba anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule+ mpaka kufika pokumbukira masiku amene anali kamtsikana,+ pamene anali kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ 20 Iye anali ndi chilakolako champhamvu ngati cha adzakazi* amene amuna awo ali ndi ziwalo ngati za abulu amphongo, amuna amene mpheto zawo zili ngati mpheto za mahatchi amphongo.+ 21 Iwe Oholiba, unapitiriza kulakalaka khalidwe lotayirira la pa utsikana wako mwa kufunafuna njira zoti amuna atsamire pachifuwa chako, kuyambira pamene unali ku Iguputo+ mpaka m’tsogolo. Unachita izi kuti ukhutiritse chilakolako cha mabere a utsikana wako.+

22 “Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndichititsa kuti amuna amene anali zibwenzi zako akuukire.+ Amenewa ndi amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo. Ine ndidzawabweretsa kuti akuukire kuchokera kumbali zonse.+ 23 Ndidzabweretsa ana aamuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa, pamodzi ndi ana aamuna a ku Asuri. Onsewa ndiwo anyamata osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri, amuna ankhondo, amuna ochita kusankhidwa ndi okwera pamahatchi. 24 Onsewa adzabwera kudzakuukira. Anthuwo pofika, padzamveka phokoso la magaleta* ankhondo ndi la mawilo.+ Iwo adzabwera ndi khamu la anthu, atatenga zishango zazikulu, zishango zazing’ono ndi zisoti. Iwo adzakuzungulira kuti akuukire. Ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, ndipo adzakuweruza motsatira malamulo awo.+ 25 Ndidzasonyeza ukali wanga pa iwe+ ndipo iwo adzakulanga mwaukali.+ Adzakuchotsa mphuno ndi makutu ndipo ziwalo zako zotsala adzazidula ndi lupanga. Iwo adzatenga+ ana ako aamuna ndi aakazi+ ndipo zinthu zako zotsala adzazitentha ndi moto.+ 26 Adzakuvula zovala zako+ ndi kutenga zinthu zako zokongola.+ 27 Ndithu, ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira mwa iwe+ ndiponso uhule wako umene unachoka nawo kudziko la Iguputo.+ Sudzakwezanso maso ako kuyang’ana amuna a ku Iguputo ndipo dziko la Iguputo sudzalikumbukiranso.’

28 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Iwe ndikupereka m’manja mwa amuna amene wadana nawo, amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo.+ 29 Iwo adzakulanga mwaukali ndi kukutengera zinthu zonse zimene unazipeza movutikira ndipo adzakusiya wosavala ndi wamaliseche.+ Umaliseche umene unauonetsa pochita dama, khalidwe lako lotayirira, ndi zochita zako zauhule zidzaonekera poyera.+ 30 Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti wachita uhule ndi mitundu ina ya anthu+ komanso chifukwa chakuti wadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+ 31 Iwe wayenda m’njira ya mkulu wako+ ndipo ndidzakupatsa kapu yake.’+

32 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Udzamwa za m’kapu ya mkulu wako, kapu yaitali ndi yaikulu.+ Udzakhala chinthu choseketsa ndi chotonzedwa chifukwa m’kapumo muli zambiri.+ 33 Udzaledzera kwambiri ndi kudzazidwa ndi chisoni. Udzaledzera ndi zinthu za m’kapu ya mkulu wako Samariya, zinthu zodabwitsa kwambiri ndi zowononga. 34 Iwe udzamwa ndi kugugudiza za m’kapuyo,+ ndipo udzatafuna zidutswa za kapuyo ndi kukhadzula mabere ako.+ “Ine ndanena,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’

35 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti wandiiwala+ ndi kundiponya kumbuyo,+ udzalangidwa chifukwa cha khalidwe lako lotayirira ndi zochita zako zauhule.’”

36 Yehova anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi uweruza+ Ohola ndi Oholiba+ ndi kuwauza zinthu zonyansa zimene achita?+ 37 Iwo achita chigololo+ ndipo m’manja mwawo muli magazi.+ Achita chigololo ndi mafano awo onyansa.+ Kuwonjezera apo, ana anga aamuna amene anandiberekera anawaponya pamoto kuti akhale chakudya cha mafanowo.+ 38 Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa+ malo anga opatulika+ ndiponso sabata langa.+ 39 Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+ 40 Kuwonjezera apo, akaziwo atatumiza uthenga kwa amuna ochokera kutali, amuna amene anawatumizira uthengawo+ anabweradi.+ Iwe unasamba,+ n’kupaka zodzikongoletsera m’maso,+ ndi kuvala zodzikongoletsera kuti amuna amenewa akuone.+ 41 Kenako unakhala pabedi pako,+ patsogolo pa tebulo loyalidwa bwino.+ Patebulopo unaikapo zofukiza zanga zonunkhira+ ndi mafuta anga.+ 42 Kumeneko kunamveka phokoso la anthu amene akucheza mosaopa kanthu.+ Kuwonjezera pa amuna ambiri amene anali kubwera, panalinso zidakwa+ zochokera m’chipululu. Amuna amenewa anaveka akaziwo zibangili ndi zisoti zokongola zachifumu kumutu kwawo.+

43 “Kenako ndinalankhula zokhudza mkazi amene anatopa chifukwa cha chigololo+ kuti, ‘Komatu apitiriza kuchita uhulewo.’+ 44 Amuna aja anapitiriza kubwera kwa iye monga mmene amuna amapitira kwa hule. Anapita kwa Ohola ndi Oholiba monga akazi akhalidwe lotayirira.+ 45 Koma amuna olungama+ ndi amene adzam’patse chiweruzo chimene amapereka kwa akazi achigololo+ komanso chimene amapereka kwa akazi okhetsa magazi.+ Pakuti iwowa ndi akazi achigololo ndipo m’manja mwawo muli magazi.+

46 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Kudzabwera khamu la anthu kudzawaukira+ ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chinthu choyenera kutengedwa ndi adani.+ 47 Khamu la anthulo lidzawaponya miyala+ ndi kuwapha ndi malupanga. Adzaphanso ana awo aamuna ndi aakazi+ ndi kutentha nyumba zawo.+ 48 Ndithu ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira+ m’dzikoli+ ndipo akazi onse adzatengerapo phunziro, moti sadzachita khalidwe lotayirira ngati lanu.+ 49 Anthu amenewo adzakulangani chifukwa cha khalidwe lanu lotayirira+ komanso mudzalangidwa chifukwa cha machimo amene munachita ndi mafano anu onyansa. Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+

24 Yehova anapitiriza kulankhula nane m’chaka cha 9, m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, lemba dzina la tsikuli. Ulembe dzina la tsiku lalero. Lero mfumu ya Babulo yazungulira mzinda wa Yerusalemu kuti iuwononge.+ 3 Nena mwambi wokhudza nyumba yopanduka.+ Unene kuti:

“‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ika pamoto mphika wakukamwa kwakukulu ndipo uthiremo madzi.+ 4 Uikemo nthuli za nyama,+ nthuli zabwinozabwino. Uikemo mwendo wam’mbuyo ndi wakutsogolo. Udzazemo mafupa abwino kwambiri. 5 Tenga nkhosa yabwino kwambiri+ ndipo usonkhezere nkhuni kuzungulira mphikawo. Uwiritse nthuli za nyamazo ndi kuphika mafupawo.”’”+

6 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi,+ umene uli ngati mphika wakukamwa kwakukulu. Mphikawo uli ndi dzimbiri ndipo dzimbiri lakelo silikutha. Muchotsemo nthulizo imodziimodzi.+ Musachite maere pamphikawo.+ 7 Pakuti magazi amene mzindawo wakhetsa ali mkati mwake.+ Waika magaziwo pathanthwe losalala, pamalo oonekera. Mzindawo sunathire magaziwo pansi kuti uwakwirire ndi dothi.+ 8 Ine ndathira magazi amene wakhetsawo pathanthwe losalala ndi loonekera kuti asakwiriridwe.+ Ndachita zimenezi kuti mkwiyo wanga uyakire mzindawo ndi kuulanga chifukwa cha zochita zake.’+

9 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi!+ Ine ndidzaunjika mulu waukulu wa nkhuni.+ 10 Sonkhanitsani zikuni zambiri. Kolezani moto. Wiritsani nyamayo mpaka ipse. Khuthulani msuzi wake ndipo mafupawo atenthe kwambiri. 11 Ikani mphikawo pamakala amoto mulibe chilichonse kuti utenthe kwambiri. Mkuwa wa mphikawo utenthe kuti zonyansa zake zisungunukemo.+ Dzimbiri lake lipse ndi moto.+ 12 Ntchito yakula. Ntchito yoyeretsa mphikawo ndi yotopetsa koma dzimbiri lake, lomwe ndi lambiri, silikuchoka.+ Uponyeni pamoto ndi dzimbiri lakelo.’

13 “‘Unachita zonyansa chifukwa cha khalidwe lako lotayirira.+ Ine ndinayesetsa kukuyeretsa, koma zonyansa zako sizinachoke.+ Sudzayeranso kufikira nditathetsera mkwiyo wanga pa iwe.+ 14 Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

15 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 16 “Iwe mwana wa munthu, ine ndimenya+ chinthu chako chokongola ndi kuchichotsa kwa iwe.+ Koma iwe usadzigugude pachifuwa, kulira kapena kugwetsa misozi.+ 17 Uuse moyo mosatulutsa mawu. Anthu akufa usawalire maliro.+ Uvale chovala chakumutu+ ndipo uvale nsapato zako.+ Usaphimbe ndevu zako zapamlomo,+ ndipo usadye chakudya chimene anthu angakupatse.”+

18 M’mawa ndinayamba kulankhula ndi anthu ndipo pofika madzulo, mkazi wanga anamwalira. Ndiyeno m’mawa ndinachita zimene anandilamula. 19 Anthu anayamba kundifunsa kuti: “Kodi sutiuza kuti zimene ukuchitazi zikutikhudza motani?”+ 20 Pamenepo ine ndinawayankha kuti: “Yehova wandiuza kuti, 21 ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri,+ chinthu chosiririka kwa inu,+ ndiponso chinthu chimene mumachichitira chifundo. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya m’mbuyo adzaphedwa ndi lupanga.+ 22 Inu mudzachita zimene ine ndachita. Simudzaphimba ndevu zanu zapamlomo+ ndipo simudzadya chakudya chimene anthu adzakupatseni.+ 23 Mudzavala chovala chakumutu ndiponso nsapato zanu. Simudzadziguguda pachifuwa kapena kulira.+ Mudzawonda chifukwa cha zolakwa zanu+ ndipo mudzabuula pakati panu.+ 24 Ezekieli wakhala chizindikiro cholosera zam’tsogolo.+ Mudzachita zonse zimene iye wachita. Mudzachita zimenezo tsoka lanu likadzafika,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”’”+

25 “Koma iwe mwana wa munthu, ine ndidzawachotsera mpanda wawo wolimba, chinthu chokongola chimene amachinyadira. Ndidzawachotsera chinthu chosiririka m’maso mwawo+ ndi chokhumba cha moyo wawo, ndiponso ana awo aamuna ndi aakazi.+ 26 Kodi pa tsiku limenelo wothawa sadzabwera kwa iwe kuti adzanene zimene zachitika?+ 27 Pa tsiku limenelo udzatsegula pakamwa pako n’kulankhula ndi wothawayo+ ndipo sudzakhalanso chete.+ Choncho iwe udzakhala chizindikiro kwa iwo cholosera zam’tsogolo,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+

25 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kwa ana a Amoni ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire.+ 3 Uuze ana a Amoniwo kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti malo anga opatulika adetsedwa, inu mwanena kuti: Eyaa! Zakhala bwino! Mwaneneranso zimenezi dziko la Isiraeli chifukwa chakuti lakhala bwinja, komanso nyumba ya Yuda chifukwa chakuti anthu ake atengedwa ukapolo.+ 4 Pa chifukwa chimenechi, ndikuperekani kwa anthu a Kum’mawa kuti mukhale chuma chawo.+ Iwo adzamanga misasa yokhala ndi mipanda ndiponso mahema awo m’dziko lanu. Adzadya zokolola zanu ndi kumwa mkaka wanu.+ 5 Mzinda wa Raba+ ndidzausandutsa malo odyetserako ngamila, ndipo dziko la ana a Amoni ndidzalisandutsa malo opumulirako gulu la nkhosa.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+

6 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti munawomba m’manja+ ndi kuponda pansi mwamphamvu, komanso munasangalala ndi mtima wonyoza poona zimene zinachitikira dziko la Isiraeli,+ 7 ine ndakutambasulirani dzanja langa,+ ndipo ndidzakuperekani kwa mitundu ina ya anthu monga zofunkha. Ndidzakuphani ndi kukuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukuwonongani kuti musapezekenso m’dziko.+ Ndidzakufafanizani,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’

8 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti Mowabu+ ndi Seiri+ anena kuti: “Taonani! Nyumba ya Yuda ili ngati mitundu ina yonse ya anthu,”+ 9 ine ndidzaonetsa adani awo malo otsetsereka a ku Mowabu. Kumalo amenewa ndi kumene kuli mizinda ya m’malire a dzikolo. Mizinda yake ndi Beti-yesimoti,+ Baala-meoni+ ndi Kiriyataimu.+ Mizinda imeneyi imakongoletsa dzikolo. 10 Ndidzapereka Mowabu limodzi ndi ana a Amoni+ kwa anthu a Kum’mawa+ kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita izi kuti ana a Amoni asadzakumbukiridwenso+ pakati pa mitundu ya anthu. 11 Ndidzapereka chiweruzo m’dziko la Mowabu,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

12 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu walanga nyumba ya Yuda ndipo akupitiriza kuilanga ndi kuichitira zinthu zoipa kwambiri,+ 13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatambasulira Edomu+ dzanja langa ndi kupha anthu ndi ziweto m’dzikolo.+ Ndidzalisandutsa bwinja kuyambira ku Temani+ mpaka ku Dedani.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga. 14 ‘Ine ndidzalanga Edomu kudzera mwa anthu anga Aisiraeli.+ Aisiraeliwo adzachitira Edomu mogwirizana ndi mkwiyo komanso ukali wanga, ndipo Aedomuwo adzadziwa mmene ndimalangira,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’

15 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Afilisiti achitira zoipa+ Aisiraeli ndipo akupitiriza kuwachitira zoipazo. Mumtima mwawo akusangalala ndiponso kuwanyoza. Akuchita zimenezi kuti awawononge+ chifukwa cha chidani chawo chomwe chidzakhalepo mpaka kalekale.+ 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ ndi kuwononga anthu onse okhala m’mbali mwa nyanja.+ 17 Anthu amenewa ndidzawalanga kwambiri ndi kuwadzudzula mwaukali,+ ndipo ndikadzawalanga adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+

26 M’chaka cha 11, pa tsiku loyamba la mwezi, Yehova analankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, Turo+ wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino! Mzindawo wathyoledwa.+ Mzinda umene unali kukopa anthu a mitundu ina+ wathyoledwa. Tsopano ine zinthu zindiyendera bwino. Ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’+ 3 Pa chifukwa chimenechi, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mitundu yambiri ya anthu+ kuti idzamenyane nawe. Anthuwo adzabwera ngati mafunde a m’nyanja.+ 4 Mitunduyo idzagwetsa mpanda wa Turo+ ndi kugumula nsanja zake.+ Ine ndidzapala fumbi lake n’kumusandutsa malo osalala opanda kanthu kalikonse, apathanthwe. 5 Iye adzakhala malo oyanikapo makoka+ pakati pa nyanja.’+

“‘Ine ndanena, anthu a mitundu ina adzalanda zinthu zake,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 6 ‘Anthu a m’midzi yake yozungulira imene ili kunja kwa mzindawo adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

7 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzatumiza Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mfumu ya mafumu,+ kuchokera kumpoto+ kuti akaukire Turo. Iye adzapita ndi mahatchi,+ magaleta ankhondo,+ asilikali a pamahatchi, khamu la anthu+ kapena kuti gulu lalikulu la anthu. 8 Anthu okhala m’midzi yozungulira imene ili kunja kwa mzindawu adzawapha ndi lupanga. Iwo adzakumangira mpanda womenyerapo nkhondo ndi chiunda chomenyerapo nkhondo,+ ndipo adzadziteteza ndi chishango chachikulu. 9 Mfumuyo idzagumula mpanda wako ndi chida chogumulira, ndipo idzagwetsa nsanja zako ndi zida zake. 10 Fumbi limene chikhamu cha mahatchi ake chidzachite lidzakufotsera.+ Mpanda wako udzagwedezeka chifukwa cha phokoso la asilikali a pamahatchi ndi mawilo a magaleta ankhondo. Izi zidzachitika iye akamadzalowa m’zipata zako ngati mmene zimakhalira polowa mumzinda umene mpanda wake augumula. 11 Ziboda za mahatchi ake zidzapondaponda m’misewu yako yonse.+ Iye adzapha anthu ako ndi lupanga ndipo zipilala zako zolimba zidzagwa. 12 Iwo adzakulanda chuma chako+ ndi malonda ako.+ Adzagwetsa mpanda wako ndi nyumba zako zosiririka. Miyala yako, zinthu zako zamatabwa ndi fumbi lako, adzaziponya m’madzi.’

13 “‘Ndidzathetsa phokoso la kuimba kwako+ ndipo phokoso la azeze ako silidzamvekanso.+ 14 Ndidzakusandutsa malo osalala apathanthwe lopanda kanthu.+ Udzakhala malo oyanikapo makoka.+ Iwe sudzamangidwanso, pakuti ine Yehova ndanena,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

15 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mzinda wa Turo kuti, ‘Kodi zilumba sizidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kuwonongedwa kwako, kubuula kwa anthu ovulazidwa koopsa, ndi kuphedwa kwa anthu ako ambiri?+ 16 Atsogoleri onse a kunyanja adzatsika+ m’mipando yawo yachifumu+ ndi kuvula malaya awo akunja odula manja. Adzavula zovala zawo za nsalu yopeta. Iwo adzavala zovala zonjenjemeretsa. Adzakhala padothi+ ndipo nthawi zonse azidzanjenjemera+ ndi kukuyang’anitsitsa modabwa. 17 Iwo adzakuimbira nyimbo yoimba polira.+ Azidzati:

“‘“Iwe mzinda wotamandika, zoona wawonongekadi! Mwa iwe munali kukhala anthu ochokera kunyanja.+ Unali wamphamvu panyanja.+ Iwe ndi anthu ako munali kuchititsa mantha anthu onse okhala padziko lapansi. 18 Pa tsiku la kuwonongedwa kwako, zilumba zidzanjenjemera. Zilumba za m’nyanja zidzasokonezeka chifukwa cha kuwonongedwa kwako.”’+

19 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndikadzakusandutsa mzinda wabwinja ngati mizinda imene simukukhala anthu, ndikadzakubweretsera madzi ambiri, ndipo madzi ochulukawo akadzakumiza,+ 20 ndidzakutsitsira m’dzenje, ngati mmene ndinatsitsira ena onse m’manda momwe muli anthu amene anafa kalekale.+ Ine ndidzakuchititsa kukhala pansi, panthaka.+ Udzakhala kumeneko pamodzi ndi malo ena amene anawonongedwa kalekale ndiponso pamodzi ndi ena onse amene akutsikira kumanda.+ Ndidzachita zimenezi kuti anthu asadzakhalenso mwa iwe, koma m’dziko la anthu amoyo ndidzaikamo zokongoletsera.+

21 “‘Ndidzakugwetsera zoopsa modzidzimutsa+ ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna+ koma sudzapezeka mpaka kalekale,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

27 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira+ yokhudza Turo. 3 Uimbire Turo kuti,

“‘Iwe amene ukukhala polowera m’nyanja,+ mkazi wochita malonda ndi anthu okhala m’zilumba zambiri,+ tamvera zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena. Iye wanena kuti: “Iwe Turo wanena kuti, ‘Ine ndine chiphadzuwa.’+ 4 Madera ako ali mkatikati mwa nyanja.+ Omwe anakupanga anakukongoletsa kwambiri.+ 5 Anakupanga ndi matabwa a mtengo wa mlombwa okhaokha ochokera ku Seniri.+ Anatenga mkungudza wa ku Lebanoni+ kuti ukhale mtengo wako womangirirapo chinsalu choyendetsera ngalawa. 6 Zopalasira ngalawa zako anazipanga ndi mitengo ikuluikulu ya ku Basana. Mbali ya kutsogolo kwako anaipanga ndi matabwa a paini, n’kuikongoletsa ndi minyanga yochokera kuzilumba za Kitimu.+ 7 Chinsalu chako choyendetsera ngalawa anachipanga ndi nsalu za mitundu yosiyanasiyana zochokera ku Iguputo.+ Pamwamba pako anaphimbapo ndi chinsalu chopangidwa ndi ulusi wabuluu+ komanso ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ wochokera kuzilumba za Elisa.+

8 “‘“Anthu a ku Sidoni+ ndi ku Arivadi+ ndi amene anali kukupalasa. Iwe Turo, anthu ako aluso+ anali mkati mwako monga ogwira ntchito m’chombo.+ 9 Amuna achikulire a ku Gebala+ ndi anthu ake aluso anali mkati mwako monga anthu omata molumikizira matabwa ako.+ Zombo zonse zapanyanja ndi oziyendetsa anali mwa iwe kuti muchite malonda ndi kusinthana zinthu. 10 Amuna a ku Perisiya,+ ku Ludi+ ndi ku Puti+ anali m’gulu lako lankhondo, anali m’gulu la asilikali ako. Amuna amenewa anali kupachika zishango ndi zisoti mwa iwe.+ Iwo ndi amene anakuchititsa kukhala waulemerero. 11 Ana aamuna a ku Arivadi+ pamodzi ndi gulu lako lankhondo anali kukhala pamwamba pa mpanda wako kuzungulira mzinda wonse. Pansanja zako panali amuna olimbikira nkhondo. Iwo anapachika zishango zawo zozungulira m’makoma ako kuzungulira mpandawo.+ Amuna amenewa anakuchititsa kuti ukhale chiphadzuwa.

12 “‘“Tarisi+ unali kuchita naye malonda a zinthu zambiri zosiyanasiyana zamtengo wapatali.+ Unamupatsa zinthu zako zimene unasunga posinthanitsa ndi siliva, chitsulo, tini ndi mtovu.+ 13 Iwe unali kuchita malonda ndi Yavani,+ Tubala+ ndi Meseke.+ Unali kuwapatsa katundu wako wogulitsa pomusinthanitsa ndi anthu+ komanso zinthu zamkuwa. 14 Unapereka zinthu zako zimene unasunga pozisinthanitsa ndi mahatchi ndi nyulu zochokera kwa ana a Togarima.+ 15 Ana a Dedani+ unali kuchita nawo malonda, ndipo unalemba ntchito zilumba zambiri kuti zizikuchitira malonda. Anthu a m’zilumbazo anali kukulipira minyanga+ komanso mitengo ya phingo. 16 Unali kuchita malonda ndi Edomu chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako. Unapereka zinthu zimene unasunga posinthanitsa ndi miyala ya nofeki,+ ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, nsalu zamitundu yosiyanasiyana, nsalu zabwino kwambiri, miyala yamtengo wapatali ya korali ndi ya rube.

17 “‘“Unali kuchita malonda ndi Yuda komanso dziko la Isiraeli. Unapereka zinthu zimene unasunga posinthanitsa+ ndi tirigu+ wa ku Miniti,+ zakudya zapamwamba, uchi,+ mafuta ndi basamu.+

18 “‘“Unali kuchita malonda ndi Damasiko+ pogulitsa katundu wambiri amene unali naye, pakuti unali ndi katundu wambiri wosiyanasiyana. Posinthana katundu, iye anakupatsa vinyo+ wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wotuwa mofiirira. 19 Vedani ndi Yavani akudera la Uzali anakupatsa katundu wawo kuti iwe uwapatse katundu amene unasunga. Iwo anakupatsa ziwiya zachitsulo, mitengo ya kasiya ndi mabango onunkhira+ posinthanitsa ndi katundu wako. 20 Dedani+ unali kuchita naye malonda a nsalu zoika pazishalo za mahatchi. 21 Unalemba ntchito Aluya+ ndi atsogoleri onse a ku Kedara+ kuti azikugulitsira malonda. Iwo anali kukugulitsira ana a nkhosa amphongo, nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+ 22 Unali kuchita malonda ndi amalonda a ku Sheba+ ndi ku Raama.+ Unali kuwapatsa zinthu zako zimene unasunga, posinthanitsa ndi mtundu ulionse wa mafuta onunkhira abwino kwambiri, mtundu uliwonse wa miyala yamtengo wapatali ndi golide.+ 23 Unali kuchita malonda ndi Harana,+ Kane, Edeni,+ amalonda a ku Sheba,+ Ashuri+ ndi Kilimadi. 24 Unali kuchita nawo malonda a zovala zokongola kwambiri, malaya akunja opangidwa ndi nsalu yabuluu komanso nsalu yamitundu yosiyanasiyana. Unalinso kuchita nawo malonda a makapeti okhala ndi mitundu iwiri ndiponso zingwe zopota zolimba kwambiri. Unali kuchita nawo malondawo pamalo ako ochitira malonda.

25 “‘“Zombo za ku Tarisi+ zoyenda m’gulu limodzi zinali kunyamula katundu wako wamalonda. Choncho unalemera ndi kukhala waulemerero kwambiri pakati pa nyanja.+

26 “‘“Anthu okupalasa akupititsa pamadzi ozama.+ Mphepo ya kum’mawa yakuwononga pakatikati pa nyanja.+ 27 Zinthu zako zamtengo wapatali, zinthu zimene unasunga,+ katundu wako wamalonda,+ anthu okuyendetsa, anthu ogwira ntchito mwa iwe,+ anthu omata molumikizira matabwa ako,+ anthu ako okugulitsira malonda, amuna ako onse ankhondo+ amene ali mwa iwe ndiponso amene ali pakati pa anthu ako onse, adzamira pakati pa nyanja pa tsiku la kuwonongedwa kwako.+

28 “‘“Chifukwa cha kufuula kwa anthu ogwira ntchito mwa iwe, dziko lonse lidzagwedezeka.+ 29 Anthu onse ogwiritsa ntchito zopalasira ngalawa, anthu oyendetsa zombo ndi anthu onse ogwira ntchito m’zombo panyanja, adzatuluka m’zombo zawo n’kukaima pamtunda.+ 30 Iwo adzakulirira mofuula ndi mowawidwa mtima.+ Adzadzithira dothi kumutu+ ndi kugubuduzika paphulusa.+ 31 Adzadzimeta mpala chifukwa cha iwe+ ndi kuvala ziguduli+ ndipo adzakulirira mowawidwa mtima.+ 32 Pokulira adzaimba nyimbo yoimba polira+ yakuti,

“‘“‘Ndani angafanane ndi Turo+ amene wawonongedwa pakati pa nyanja?+ 33 Zinthu zimene unasunga+ zikafika kumtunda+ zinali kukwanira mitundu yambiri ya anthu.+ Mafumu a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zako zochuluka zamtengo wapatali ndi katundu wako wogulitsa.+ 34 Tsopano nyanja yakuwononga, ndipo wamira m’madzi ozama.+ Katundu wako wamalonda ndi khamu la anthu+ limene linali mwa iwe zatheratu. 35 Anthu onse okhala m’zilumba+ adzakuyang’anitsitsa modabwa ndipo mafumu awo adzanjenjemera chifukwa cha mantha.+ Nkhope zawo zonse zidzaoneka zankhawa.+ 36 Amalonda ochokera pakati pa mitundu ina ya anthu adzakuimbira miluzu.+ Zoopsa zodzidzimutsa zidzakugwera ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.’”’”+

28 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:

“‘“Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ndipo ukunena kuti, ‘Ndine mulungu.+ Ndakhala pampando wa mulungu+ pakatikati pa nyanja,’+ ngakhale kuti ndiwe munthu wochokera kufumbi+ osati mulungu,+ ndipo umadziona ngati mulungu . . . 3 iwe umaganiza kuti ndiwe wanzeru kuposa Danieli.+ Umaganiza kuti palibe chinsinsi chimene sukuchidziwa.+ 4 Chifukwa chakuti ndiwe wanzeru ndiponso wozindikira, wapanga chuma ndipo ukupitiriza kusonkhanitsa golide ndi siliva m’nyumba zako zosungiramo zinthu.+ 5 Wachulukitsa chuma chako+ chifukwa chakuti uli ndi nzeru zochuluka+ komanso umachita malonda.+ Chotero mtima wako wayamba kudzikuza chifukwa cha chuma chakocho.”’+

6 “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti umadziona ngati mulungu,+ 7 ine ndikubweretsera alendo,+ anthu ankhanza a mitundu ina.+ Iwo adzasolola lupanga n’kuwononga chilichonse chokongola chimene unapeza chifukwa cha nzeru zako, ndipo adzaipitsa ulemerero wako wonyezimira.+ 8 Adzakutsitsira kudzenje.+ Udzafa ngati munthu wophedwa ndi lupanga pakatikati pa nyanja.+ 9 Kodi amene adzakuphe udzamuuza kuti, ‘Ine ndine mulungu,’+ pamene ndiwe munthu wamba wochokera kufumbi osati mulungu?+ Kodi udzanena zimenezi m’manja mwa okuipitsawo?”’

10 “‘Udzafa ngati anthu osadulidwa ndipo alendo ndi amene adzakuphe,+ ine ndanena,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

11 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo.+ Uuze mfumuyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:

“‘“Ndiwe chitsanzo changwiro. Uli ndi nzeru zochuluka+ ndipo ndiwe wokongola kwambiri.+ 13 Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu.+ Unali kuvala chovala chokongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse monga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi,+ yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi. Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide. Anakukonzera zimenezi pa tsiku limene unalengedwa. 14 Iwe ndiwe kerubi wodzozedwa amene umagwira ntchito yoteteza, ndipo ine ndakuika pa udindo. Unali kukhala paphiri loyera la Mulungu.+ Unali kuyendayenda pamiyala yamoto. 15 Unali wopanda cholakwa m’njira zako kuchokera pa tsiku limene unalengedwa,+ kufikira pamene unachita zinthu zosalungama.+

16 “‘“Chifukwa cha kuchuluka kwa malonda ako,+ mwa iwe munadzaza zachiwawa ndipo unayamba kuchita machimo.+ Iwe kerubi amene umagwira ntchito yoteteza, ine ndidzakutulutsa m’phiri la Mulungu monga wodetsedwa ndipo ndidzakuwononga pakati pa miyala yamoto.+

17 “‘“Mtima wako unadzikweza chifukwa cha kukongola kwako.+ Unawononga nzeru zako chifukwa cha ulemerero wako wonyezimira.+ Ndidzakuponyera kudziko lapansi+ ndipo mafumu azidzakuyang’ana.+

18 “‘“Chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako,+ chifukwa cha malonda ako opanda chilungamo,+ waipitsa malo ako opatulika. Ndidzabweretsa moto kuchokera pakati pako, ndipo udzakunyeketsa.+ Ndidzakusandutsa phulusa padziko lapansi pamaso pa anthu onse okuona.+ 19 Onse okudziwa pakati pa mitundu ya anthu adzakuyang’anitsitsa modabwa.+ Zoopsa zodzidzimutsa zidzakugwera ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.”’”+

20 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana ku Sidoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire. 22 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe Sidoni, ine ndithana nawe+ ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako.+ Ndikadzapereka ziweruzo mwa iwe ndi kuyeretsedwa kudzera mwa iwe,+ anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 23 Ndidzakutumizira miliri ndipo magazi adzayenderera m’misewu yako.+ Anthu ophedwa adzapezeka paliponse mwa iwe. Iwo adzaphedwa ndi lupanga lochokera kumbali zonse,+ moti anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 24 Nyumba ya Isiraeli sidzalasidwanso ndi cholasa chopweteka+ kapena minga zaululu zochokera kwa onse owazungulira, amene akuwatonza, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’

25 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+ 26 Adzakhala m’dzikolo popanda chowaopseza,+ adzamanga nyumba+ ndi kulima minda ya mpesa.+ Iwo adzakhala mwabata+ ndikadzapereka chiweruzo kwa onse owazungulira amene akuwatonza.+ Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo.”’”

29 M’chaka cha 10, m’mwezi wa 10, pa tsiku la 12 la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kwa Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire iyeyo ndi dziko lonse la Iguputo.+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndilanga iwe Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndiwe chilombo chachikulu cha m’nyanja+ chimene chagona m’ngalande zake zotuluka mumtsinje wa Nailo.+ Ndiwe chilombo chimene chanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+ 4 Ndidzakukola ndi ngowe munsagwada zako+ ndi kuchititsa nsomba za m’ngalande za mtsinje wa Nailo kukakamira kumamba ako. Ndidzakutulutsa m’ngalande za Nailo pamodzi ndi nsomba zonse za m’ngalandezo zimene zakakamira kumamba ako. 5 Iwe ndidzakutaya m’chipululu pamodzi ndi nsomba zonse za m’ngalande za Nailo.+ Udzagwera panthaka+ ndipo palibe amene adzakutenge kukakuika m’manda. Ndidzakupereka kwa zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka kuti ukhale chakudya chawo.+ 6 Anthu onse okhala ku Iguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova+ chifukwa chakuti iwo anali ngati bango loyendera la nyumba ya Isiraeli.+ 7 Atakugwira dzanja ndi kukutsamira ngati ndodo yoyendera, unaphwanyika+ ndipo unachititsa kuti miyendo* yawo ikhale yagwedegwede,+ zimene zinawachititsa kuti athyole+ phewa lawo.”

8 “‘Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndibweretsa lupanga+ m’dziko lako ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto.+ 9 Dziko la Iguputo lidzakhala bwinja ndi malo owonongeka.+ Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova chifukwa chakuti iwe Farao wanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+ 10 Choncho, iwe ndikulanga ndi kuwononga ngalande zako zotuluka mu Nailo.+ Dziko la Iguputo ndiliwononga. Ndilisandutsa malo ouma komanso bwinja,+ kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene+ kukafika kumalire a dziko la Itiyopiya. 11 M’dziko lako simudzaponda phazi la munthu+ kapena la chiweto,+ ndipo simudzakhala munthu aliyense kwa zaka 40.+ 12 Dziko la Iguputo ndidzalisandutsa bwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu.+ Kwa zaka 40, mizinda yake idzakhala mabwinja pakati pa mizinda yopanda anthu.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira m’mayiko ena.”+

13 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Zaka 40 zikadzatha,+ ndidzasonkhanitsa pamodzi Aiguputowo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina kumene adzabalalikire.+ 14 Ndidzabwezeretsa gulu la Aiguputo amene anagwidwa n’kupita nawo kudziko lina. Ndidzawabwezeretsa kudera la Patirosi,+ m’dziko limene anachokera. Kumeneko adzakhazikitsa ufumu wonyozeka. 15 Ufumu wawo udzakhala wotsika kusiyana ndi maufumu ena ndipo sudzadzikwezanso pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndidzawachepetsa kwambiri moti sadzakhalanso ndi mphamvu zolamulira mitundu ina ya anthu.+ 16 Nyumba ya Isiraeli sidzawadaliranso.+ Aisiraeli sadzachititsa kuti zolakwa zawo zikumbukiridwe mwa kutembenukira kwa Iguputo,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”

17 Tsopano m’chaka cha 27, m’mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, Nebukadirezara+ mfumu ya Babulo anatuma gulu lake lankhondo kukachita utumiki wofunika kwambiri pomenyana ndi Turo.+ Mutu wa msilikali aliyense unameteka ndipo mapewa awo ananyuka.+ Koma mfumuyo ndi gulu lake lankhondo sanalandire cholowa+ chilichonse pa utumiki umene anachita pomenyana ndi Turo.

19 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndipereka dziko la Iguputo kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo.+ Adzatenga chuma chake chochuluka ndi kulanda zinthu zake zambiri.+ Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.’

20 “‘Ndamupatsa dziko la Iguputo monga chipukutamisozi pa utumiki wake umene anachita pomenyana ndi Turo, chifukwa iwo anachita zimene ine ndinali kufuna,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

21 “Pa tsikulo, ndidzaphukitsira nyumba ya Isiraeli nyanga.*+ Iwe ndidzakupatsa mpata kuti utsegule pakamwa pako pakati pawo,+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”

30 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Fuulani anthu inu kuti, ‘Kalanga ine! Tsiku lija layandikira.’+ 3 Tsikulo lili pafupi. Inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Limeneli lidzakhala tsiku la mitambo,+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+ 4 Lupanga lidzafikadi mu Iguputo,+ ndipo ku Itiyopiya anthu adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitika anthu akadzaphedwa mu Iguputo, chuma cha dzikolo chikadzalandidwa komanso maziko ake akadzagwetsedwa.+ 5 Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera ku mitundu ina,+ Kubi ndi anthu ochokera m’dziko la Isiraeli amene ali m’pangano, onsewa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Aiguputo.”’+

6 “Yehova wanena kuti, ‘Nawonso othandiza Iguputo adzaphedwa, ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.’+

“‘Kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene,+ anthu adzaphedwa ndi lupanga m’dzikolo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 7 ‘Onsewo adzakhala mabwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu ndipo mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yowonongedwa.+ 8 Ndikadzayatsa moto mu Iguputo, ndipo onse omuthandiza akadzawonongedwa, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 9 Pa tsikulo, amithenga ochokera kwa ine adzakwera zombo kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira.+ Itiyopiya adzamva ululu woopsa pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, pakuti tsikulo lidzafika ndithu.’+

10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+ 11 Mfumuyo ndi anthu ake, olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu,+ akubwera kudzawononga dzikolo kuti likhale bwinja. Iwo adzasolola malupanga awo kumenyana ndi Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+ 12 Ndidzaumitsa ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo+ ndi kugulitsa dzikolo kwa anthu oipa.+ Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu achilendo.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’+

13 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononganso mafano onyansa+ ndi kuthetsa milungu yopanda pake ku Nofi.+ Sipadzapezekanso mtsogoleri wochokera m’dziko la Iguputo, ndipo ndidzachititsa anthu a m’dzikolo kukhala mwamantha.+ 14 Mzinda wa Patirosi+ ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani+ ndidzautentha ndi moto ndipo ndidzapereka ziweruzo mumzinda wa No.+ 15 Ndidzatsanulira mkwiyo wanga+ pa Sini, malo otetezedwa kwambiri a Iguputo, ndipo ndidzapha khamu la anthu a ku No.+ 16 Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzamva ululu waukulu, No adzalandidwa ndi adani amene adzagumule mpanda wake. Adani adzalowa mumzinda wa Nofi masanasana. 17 Anyamata a ku Oni+ ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga. Anthu a m’mizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo. 18 Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 19 Ndidzapereka ziweruzo mu Iguputo+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

20 Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova analankhulanso ndi ine kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo.+ Dzanjalo silidzamangidwa ndi nsalu zomangira pachilonda+ kuti lichire n’kukhalanso lamphamvu kuti lizidzatha kugwira lupanga.”

22 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndidzathyola manja ake onse,+ dzanja lamphamvu ndi lothyoka lija,+ ndipo ndidzachititsa kuti lupanga ligwe m’dzanja lake.+ 23 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu ndi kuwamwazira kumayiko ena.+ 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa.+ Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri pamaso pa mfumu ya Babulo monga wovulazidwa koopsa.+ 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo ndipo Farao adzagwetsa manja ake. Ndikadzapereka lupanga langa m’manja mwa mfumu ya Babulo, iye n’kuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 26 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu+ ndi kuwamwazira kumayiko ena, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

31 Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi wachitatu, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza Farao mfumu ya Iguputo ndi khamu lake kuti,+

“‘Kodi wakula kufanana ndi ndani? 3 Wafanana ndi Msuri. Wafanana ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,+ wanthambi zikuluzikulu zokongola,+ wanthambi za masamba ambiri zopereka mthunzi, mtengo wautali kwambiri+ umene nsonga yake inafika m’mitambo.+ 4 Mtengowo unakula kwambiri chifukwa cha madzi.+ Unatalika chifukwa cha madzi akuya. Madziwo anali kuyenda m’mitsinje kuzungulira pamalo pamene mtengowo unabzalidwa. Ngalande za madziwo zinakafika kumitengo yonse ya kumeneko. 5 N’chifukwa chake mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo yonse yakumaloko.+

“‘Nthambi zake zikuluzikulu zinali kuchuluka, ndipo nthambi zina zinapitiriza kutalika chifukwa cha kuchuluka kwa madzi m’ngalande zake.+ 6 Zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zinali kumanga zisa zawo m’nthambi zake zikuluzikuluzo.+ Nyama zonse zakutchire zinkaberekera pansi pa nthambi zake.+ Mitundu yonse ya anthu ambiri inali kukhala mumthunzi wake. 7 Mtengowo unakongola kwambiri+ chifukwa cha kukula kwake ndi kutalika kwa nthambi zake zamasamba ambiri. Izi zinachitika chifukwa chakuti mizu yake inali pamadzi ambiri. 8 Mitengo ina ya mkungudza sinafanane ndi mtengo umenewu m’munda wa Mulungu.+ Nthambi zikuluzikulu za mitengo ina yooneka ngati mkungudza, sizinafanane ndi za mtengo umenewu. Nthambi za mitengo ya katungulume sizinafanane ndi nthambi za mtengo umenewu. Panalibenso mtengo wina m’munda wa Mulungu umene unali wokongola ngati mtengo umenewu.+ 9 Mtengo umenewu ndinaukongoletsa pouchulukitsira nthambi zamasamba ambiri.+ Mitengo ina yonse ya mu Edeni, imene inali m’munda wa Mulungu woona, inali kuuchitira nsanje.’+

10 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti mtengowu unatalika kwambiri moti nsonga yake inakafika m’mitambo,+ ndipo mtima wake unayamba kudzikuza chifukwa cha kutalika kwake,+ 11 ndidzaupereka m’manja mwa wolamulira wamphamvu wa mitundu ina.+ Iye adzaukhaulitsa, ndipo chifukwa cha kuipa kwake ine ndidzauthamangitsa.+ 12 Anthu achilendo, olamulira ankhanza a mitundu ina, adzadula mtengowo ndipo anthu adzausiya m’mapiri. Masamba ake adzagwera m’zigwa zonse ndipo nthambi zake zidzathyoka ndi kugwera m’mitsinje ya padziko lapansi.+ Mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi idzachoka mumthunzi wake n’kuusiya.+ 13 Zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zidzakhala pathunthu lake logwetsedwalo, ndipo nyama zonse zakutchire zidzakhala m’nthambi zake.+ 14 Choncho sipadzakhalanso mtengo uliwonse wothiriridwa bwino umene udzakhale wautali kwambiri kapena umene nsonga zake zidzafike m’mitambo. Sipadzakhala mtengo uliwonse umene uli pamadzi ambiri umene udzatalike kukafika m’mitambo, pakuti mitengo yonse idzakhala itadulidwa.+ Yonse idzakhala itatsikira pansi pa nthaka+ pamodzi ndi ana a anthu amene akutsikira kudzenje.’

15 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limene mtengo wamkungudza udzatsikire ku Manda* ndidzachititsa anthu kulira.+ Ndidzaphimba madzi akuya chifukwa cha mtengowo. Ndidzachita izi kuti ndiimitse madzi m’mitsinje yake ndi kutseka madzi ambiri. Ndidzachititsa mdima mu Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse yakutchire idzafota. 16 Mitundu ya anthu ikadzamva phokoso la kugwa kwake idzanjenjemera. Zimenezi zidzachitika ndikadzatsitsira mtengowo ku Manda pamodzi ndi amene akutsikira kudzenje.+ Mitengo yonse ya mu Edeni+ imene ili pansi pa nthaka, mitengo yabwino kwambiri ya ku Lebanoni ndi mitengo yonse imene inali pamadzi ambiri, idzatonthozedwa.+ 17 Mitengo imeneyi yatsikira ku Manda pamodzi ndi mtengo wa mkungudzawo.+ Yatsikira kwa ophedwa ndi lupanga ndi kwa amene ankakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ina ya anthu monga mbewu yake.’+

18 “‘Kodi iwe ukufanana ndi ndani pa nkhani ya ulemerero+ ndi kukula pakati pa mitengo ya mu Edeni?+ Koma ndithu udzatsikira pansi pa nthaka limodzi ndi mitengo ya mu Edeni.+ Udzagona pakati pa anthu osadulidwa limodzi ndi ophedwa ndi lupanga. Mtengo umenewu ukuimira Farao ndi khamu lake lonse,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

32 M’chaka cha 12, m’mwezi wa 12, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nanenso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Farao, mfumu ya Iguputo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Iwe wawonongedwa ngakhale kuti unali ngati mkango wamphamvu pakati pa mitundu ina ya anthu.+

“‘Unali ngati chilombo cham’nyanja.+ Nthawi zonse unali kuyenda mwamphamvu ngati madzi m’mitsinje yako, ndipo unali kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa mitsinjeyo.’

3 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzakuphimba ndi ukonde+ wanga pogwiritsa ntchito khamu la anthu ambiri a mitundu ina, ndipo iwo adzakukola ndi khoka langa.+ 4 Ndidzakusiya pamtunda ndiponso ndidzakuponya kuchigwa.+ Ndidzachititsa kuti zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zitere pa iwe. Ndidzakhutitsa zilombo zakutchire ndi nyama yako.+ 5 Mnofu wako ndidzauika m’mapiri, ndipo m’zigwa ndidzadzazamo zotsalira za mtembo wako.+ 6 Ndidzachititsa dziko kumwa zinthu zotuluka m’thupi mwako. Ndidzalichititsa kumwa magazi+ ako m’mapiri. Mitsinje idzadzaza ndi zinthu zotuluka m’thupi mwako.’

7 “‘Ndikadzakuzimitsa, ndidzaphimba kumwamba n’kuchititsa mdima nyenyezi zake. Dzuwa ndidzaliphimba ndi mitambo ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.+ 8 Zounikira zonse zakumwamba ndidzazichititsa mdima chifukwa cha iwe, ndipo ndidzagwetsa mdima m’dziko lako,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

9 “‘Ndidzakhumudwitsa mitima ya anthu ambiri a mitundu ina ndikadzatenga ena mwa anthu ako ndi kuwapititsa kudziko lina, kwa anthu a mitundu ina, kumayiko amene sukuwadziwa.+ 10 Ndidzachititsa mantha anthu ambiri a mitundu ina chifukwa cha iwe.+ Ndikadzawaloza ndi lupanga langa kumaso,+ mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha. Kuyambira pa tsiku limene udzaphedwe, aliyense wa iwo azidzanjenjemera nthawi zonse chifukwa choopa kufa.’+

11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Lupanga la mfumu ya Babulo lidzafika pa iwe.+ 12 Ndidzachititsa khamu la anthu ako kuphedwa ndi malupanga a anthu amphamvu. Anthu onsewo ndi olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu.+ Iwo adzawononga zonse zimene Iguputo amazinyadira ndipo khamu lake lonse lidzawonongedwa.+ 13 Ndidzawononga ziweto zake zonse ndi kuzichotsa m’mbali mwa madzi.+ Phazi la munthu komanso ziboda za chiweto sizidzavundulanso madziwo.’+

14 “‘Pa nthawi imeneyo ndidzayeretsa madzi awo, ndipo madzi a m’mitsinje yawo adzayenda ngati mafuta,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

15 “‘Ndikadzasandutsa dziko la Iguputo bwinja ndipo zinthu zonse za m’dzikolo zikadzawonongedwa,+ komanso ndikadzapha anthu onse okhala m’dzikolo, anthu a mitundu ina adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+

16 “‘Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo anthu adzaiimba. Ana aakazi a mitundu ina ya anthu adzaiimba. Nyimbo imeneyi adzaimbira Iguputo ndi khamu lake lonse,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

17 M’chaka cha 12, pa tsiku la 15 la mwezi, Yehova analankhula nanenso kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira khamu la ku Iguputo ndi kulengeza kuti lidzatsikira kumanda.+ Dzikolo ndi anthu a mitundu yamphamvu adzatsikira pansi pa nthaka+ limodzi ndi amene akutsikira kudzenje.+

19 “‘Kodi ndiwe wosangalatsa kwambiri kuposa ndani?+ Tsikira kumanda ndipo uikidwa limodzi ndi anthu osadulidwa.’+

20 “‘Aiguputo adzaphedwa pamodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga.+ Dzikolo laperekedwa ku lupanga. Anthu inu, kokerani kutali dzikolo ndi khamu lake lonse.

21 “‘Ku Mandako, atsogoleri a anthu amphamvu adzalankhula ndi iyeyo komanso amene anali kumuthandiza.+ Onsewo adzatsikira kumanda.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzaikidwa m’manda mofanana ndi anthu osadulidwa. 22 Kumeneko n’kumene kuli Asuri ndi khamu lake lonse.+ Manda a anthu a ku Asuri ali mozungulira mfumu yawo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga.+ 23 Manda a Asuri ali pakatikati pa dzenje+ ndipo khamu lake lonse lazungulira manda akewo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.

24 “‘Kumandako n’kumene kuli Elamu+ ndi khamu lake lonse. Khamu lakelo linaikidwa mozungulira manda ake. Onsewo anaphedwa ndi lupanga. Iwo anatsikira kunthaka ali osadulidwa. Amenewa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo, ndipo adzanyozeka limodzi ndi onse otsikira kudzenje.+ 25 Bedi lake aliika pakati pa anthu ophedwa,+ aliika pakati pa khamu lake lonse. Manda a anthu ake azungulira bedilo. Onsewo ndi anthu osadulidwa, ophedwa ndi lupanga+ chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo. Adzanyozeka limodzi ndi amene akutsikira kudzenje. Iye waikidwa m’manda pakati pa anthu ophedwa.

26 “‘Kumeneko kulinso dziko la Meseke,+ Tubala+ ndi makamu awo onse. Manda awo ali mozungulira mfumu yawo. Onsewa ndi anthu osadulidwa, anthu olasidwa ndi lupanga chifukwa chakuti anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo. 27 Kodi amenewa sadzagona limodzi ndi anthu amphamvu+ amene anaphedwa pakati pa anthu osadulidwa? Kodi sadzagona limodzi ndi anthu amene anatsikira ku Manda limodzi ndi zida zawo zankhondo? Mitu yawo idzatsamira malupanga awo ndipo mafupa awo adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa anthu amphamvuwo anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.+ 28 Koma iwe udzathyoledwa pakati pa anthu osadulidwa ndipo udzagona limodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga.

29 “‘Kumeneko n’kumene kuli Edomu,+ mafumu ake ndi atsogoleri ake onse. Amenewa anaikidwa m’manda akadali amphamvu. Anaikidwa pamodzi ndi ophedwa ndi lupanga.+ Iwo adzagona limodzi ndi anthu osadulidwa+ komanso anthu amene akutsikira kudzenje.

30 “‘Kumeneko n’kumene kuli nduna zonse za kumpoto. Kulinso Asidoni+ onse amene anatsikira kumanda ali amanyazi. Anatsikira kumeneko limodzi ndi ophedwa, ngakhale kuti anali ochititsa mantha chifukwa cha mphamvu zawo. Adzagona m’manda limodzi ndi ophedwa ndi lupanga ali osadulidwa. Iwo adzachita manyazi pamodzi ndi otsikira kudzenje.+

31 “‘Amenewa ndiwo anthu amene Farao adzawaone ndipo mtima wake udzakhala pansi poona khamu lake lonse.+ Farao ndi gulu lake lonse lankhondo adzakhala m’gulu la anthu ophedwa ndi lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

32 “‘Zimenezi zidzamuchitikira chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.+ Farao ndi khamu lake lonse adzaikidwa m’manda pakati pa anthu osadulidwa. Iye adzaikidwa m’manda pamodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

33 Yehova analankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi anthu a mtundu wako+ ndipo uwauze kuti,

“‘Ndikabweretsa lupanga m’dziko,+ ndipo mogwirizana anthu a m’dzikolo akasankha munthu kuti akhale mlonda wawo,+ 3 mlondayo akaona lupanga likubwera m’dzikomo iye n’kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa kuchenjeza anthu,+ 4 munthu akamva kulira kwa lipengalo koma osachitapo kanthu,+ lupanga n’kubwera ndi kumupha, magazi ake adzakhala pamutu pake.+ 5 Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire chenjezolo. Magazi ake adzakhala pamutu pake. Ngati iye akanalabadira chenjezo, akanapulumutsa moyo wake.+

6 “‘Koma mlondayo akaona lupanga likubwera, iye osaliza lipenga,+ anthu osamva chenjezo lililonse, lupangalo n’kufika ndi kupha anthu, anthuwo adzaphedwa chifukwa cha zolakwa zawo,+ koma magazi awo ndidzawafuna kuchokera m’manja mwa mlondayo.’+

7 “Koma iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Umve mawu ochokera pakamwa panga ndi kundichenjezera anthuwo.+ 8 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa ndithu,’+ koma iwe osanena mawu alionse ochenjeza woipayo kuti asiye njira yake,+ iyeyo poti ndi woipa adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera m’manja mwako. 9 Koma iweyo ukachenjeza munthu woipa kuti asiye njira zake ndi kubwerera, koma iye osasiya njira zake zoipa ndi kubwerera, munthuyo adzafa chifukwa cha zoipa zake.+ Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.+

10 “Choncho iwe mwana wa munthu, uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Anthu inu mwanena kuti: “Tingakhale bwanji ndi moyo, popeza kuti kupanduka kwathu ndi machimo athu zili pa ife ndipo tikuwola+ chifukwa cha zimenezi?”’+ 11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere+ kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+

12 “Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako kuti, ‘Munthu wolungama akapanduka, chilungamo chake sichidzamupulumutsa pa tsiku la kupanduka kwake.+ Koma munthu woipa akabwerera n’kusiya zoipa zakezo, sadzafa chifukwa cha zoipazo pa tsiku limene adzabwerere n’kuzisiya.+ Komanso munthu wolungama sadzakhalabe ndi moyo chifukwa cha chilungamo chake pa tsiku limene adzachimwe.+ 13 Ndikauza munthu wolungama kuti: “Iwe udzakhalabe ndi moyo,” ndiyeno iyeyo n’kudalira kwambiri kulungama kwakeko n’kuchita zinthu zopanda chilungamo,+ zochita zake zonse zolungama zija sizidzakumbukiridwa. Iye adzafa chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene anachita.+

14 “‘Ndikauza munthu woipa kuti: “Udzafa ndithu,”+ ndiyeno iye n’kubwerera kusiya machimo akewo,+ n’kuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ 15 akabweza chinthu chimene anatenga kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ akabweza zinthu zimene analanda mwauchifwamba,+ n’kuyamba kuyenda motsatira malamulo opatsa moyo mwa kupewa kuchita zinthu zopanda chilungamo,+ munthuyo adzakhalabe ndi moyo,+ sadzafa ayi. 16 Palibe tchimo ngakhale limodzi mwa machimo onse amene anachita limene lidzakumbukiridwe ndi kumulanga nalo.+ Iye anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo. Choncho adzakhalabe ndi moyo.’+

17 “Anthu a mtundu wako anena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo,’+ komatu njira zawo ndiye zopanda chilungamo.

18 “Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ayenera kufa chifukwa cha zochita zakezo.+ 19 Munthu woipa akasiya kuchita zinthu zoipa n’kuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, adzakhalabe ndi moyo chifukwa cha zochita zake zolungamazo.+

20 “Anthu inu mwanena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake.”+

21 Ndiyeno m’chaka cha 12 kuchokera pamene tinatengedwa ukapolo, m’mwezi wa 10, pa tsiku lachisanu la mweziwo, kunafika munthu amene anapulumuka kuchokera ku Yerusalemu. Iye anandiuza+ kuti: “Mzinda uja wawonongedwa!”+

22 Tsopano madzulo, munthu wopulumuka uja asanafike, dzanja la Yehova linandikhudza.+ Ndipo Mulungu anatsegula pakamwa panga, wopulumuka uja asanafike m’mawa. Pakamwa panga panatseguka ndipo ndinayambanso kulankhula.+

23 Yehova anayamba kundiuza kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, anthu okhala m’malo owonongedwa+ akulankhula za dziko la Isiraeli kuti, ‘Abulahamu anali munthu mmodzi koma anatenga dzikoli.+ Ife tilipo ambiri, choncho dzikoli laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’+

25 “Choncho auze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mumadya nyama limodzi ndi magazi ake,+ mumayang’anitsitsa mafano anu onyansa+ ndipo mumakhetsa magazi.+ Kodi pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu?+ 26 Mumadalira lupanga lanu.+ Mwachita zinthu zonyansa+ ndipo aliyense wa inu waipitsa mkazi wa mnzake.+ Kodi pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu?”’+

27 “Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndithu anthu amene ali m’malo owonongedwa adzaphedwa ndi lupanga.+ Munthu amene ali kutchire ndidzam’pereka kwa chilombo cholusa kuti akhale chakudya chake.+ Anthu amene ali m’malo otetezeka ndi m’mapanga+ adzafa ndi mliri. 28 Dzikolo ndidzalisandutsa bwinja+ ndiponso malo owonongeka. Ndidzathetsa mphamvu zimene dzikolo limanyadira.+ Mapiri a mu Isiraeli adzawonongedwa+ ndipo sipadzapezeka wodutsamo. 29 Dzikolo ndikadzalisandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene achita,+ iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’

30 “Koma iwe mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akukambirana za iwe m’mbali mwa mpanda ndi m’makomo a nyumba.+ Aliyense akuuza m’bale wake kuti, ‘Bwerani mudzamve mawu a Yehova.’+ 31 Iwo adzabwera kwa iwe ngati mmene amachitira nthawi zonse ndipo adzakhala pamaso pako ngati anthu anga.+ Adzamva mawu ako koma sadzawatsatira,+ chifukwa ndi pakamwa pawo, akulankhula za zilakolako zawo zonyansa ndipo mtima wawo uli pa kupeza phindu mopanda chilungamo.+ 32 Kwa iwo uli ngati munthu woimba nyimbo zachikondi. Uli ngati munthu wa mawu anthetemya komanso wodziwa kuimba choimbira cha zingwe.+ Iwo adzamva ndithu mawu ako, koma palibe amene adzawatsatire.+ 33 Koma mawu ako akadzakwaniritsidwa, pakuti adzakwaniritsidwa ndithu,+ iwo adzadziwa kuti pakati pawo panalidi mneneri.”+

34 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire abusa a Isiraeli. Losera, ndipo uuze abusawo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka abusa a Isiraeli,+ amene akungodzidyetsa okha!+ Kodi abusa ntchito yawo si kudyetsa nkhosa?+ 3 Inu mukudya mafuta,+ ndipo mukuvala zovala zaubweya wa nkhosa. Mukupha+ nyama zonenepa,+ koma nkhosa simukuzidyetsa. 4 Nkhosa zodwala simunazilimbitse+ ndipo zamatenda simunazichiritse. Yothyoka mwendo simunaimange mwendo wothyokawo. Nkhosa zomwazika simunazibweze ndipo zosochera simunazifufuze kuti muzipeze.+ Munali kuzilamulira mouma mtima komanso mwankhanza.+ 5 Pang’ono ndi pang’ono zinamwazikana chifukwa chakuti zinalibe m’busa.+ Choncho zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire ndipo zinapitiriza kumwazikana.+ 6 Nkhosa zanga+ zinasochera m’mapiri onse ndi m’zitunda zonse zitalizitali.+ Zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wozifufuza ndi kuziyang’anayang’ana.

7 “‘“Choncho abusa inu, imvani mawu a Yehova. 8 ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “nkhosa zanga zinali kungobedwa ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire. Nkhosa zanga zinalibe m’busa, ndipo abusa anga sanazifunefune koma anali kumangodzidyetsa okha,+ osadyetsa nkhosa zanga.”’ 9 Chotero abusa inu, imvani mawu a Yehova. 10 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi ine ndilanga abusawo.+ Ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga ndipo ndiwaletsa kudyetsa nkhosa zangazo.+ Abusawo sadzadzidyetsanso okha.+ Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwawo ndipo sizidzakhalanso chakudya chawo.’”+

11 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.+ 12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mmene amachitira munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa+ zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika.+ Pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani, ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.+ 13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa+ pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko ena ndi kuzibweretsa m’dziko lawo.+ Ndidzazidyetsa m’mapiri a ku Isiraeli, m’mphepete mwa mitsinje komanso m’malo onse a m’dzikolo okhalako anthu.+ 14 Nkhosazo ndidzazidyetsera m’malo a msipu wabwino ndipo zizidzakhala m’mapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi m’malo abwino kwambiri.+ Zizidzadya msipu wobiriwira bwino m’mapiri a ku Isiraeli.”

15 “‘“Ine ndidzadyetsa nkhosa zanga,+ ndipo ndidzazigonetsa pansi,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna,+ zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa, koma yonenepa+ ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo monga chakudya chake.”+

17 “‘Koma inu nkhosa zanga, imvani zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena. Iye wanena kuti: “Ine ndidzaweruza mwachilungamo pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake komanso pakati pa nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+ 18 Kodi mukuona ngati n’chinthu chaching’ono kuti inu muzidya msipu wabwino kwambiri+ koma msipu wotsala n’kuupondaponda ndi mapazi anu? Kodi mukuona ngati n’chinthu chaching’ono kuti inu muzimwa madzi oyera koma madzi otsala muziwadetsa mwa kuwapondaponda ndi mapazi anu? 19 Kodi nkhosa zanga zizidya msipu wa pamalo odyetserapo ziweto umene inu mwaupondaponda ndi mapazi anu? Kodi zizimwa madzi amene mwawadetsa powapondaponda ndi mapazi anu?”

20 “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa iwo kuti: “Ndithu ine ndidzapereka chiweruzo pakati pa nkhosa yonenepa ndi nkhosa yowonda. 21 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti munali kukankha nkhosa ndi nthiti zanu ndiponso mapewa anu. Munali kugunda ndi nyanga zanu nkhosa zonse zodwala mpaka kuzibalalitsira kunja.+ 22 Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sizidzabedwanso.+ Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake. 23 Ndidzazipatsa m’busa mmodzi,+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala m’busa wawo ndipo adzazidyetsadi.+ 24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wawo,+ ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri pakati pawo.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.

25 “‘“Ine ndidzachita nazo pangano la mtendere.+ Ndidzachotsa zilombo zolusa zakutchire m’dzikomo.+ Nkhosazo zidzakhala m’chipululu popanda choziopsa ndipo zizidzagona m’nkhalango.+ 26 Nkhosazo komanso malo ozungulira phiri langa ndidzawasandutsa dalitso.+ Ndidzagwetsa mvula yambiri pa nthawi yake. Kudzagwa mvula yambiri yamadalitso.+ 27 Mtengo wam’munda udzabereka zipatso.+ Nthaka idzatulutsa zokolola zake.+ Iwo adzakhala m’dziko lawo mwabata.+ Ndikadzathyola goli lawo+ ndi kuwapulumutsa m’dzanja la amene anali kuwagwiritsa ntchito monga akapolo,+ adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 28 Iwo sadzabedwanso ndi anthu a mitundu ina.+ Chilombo chakutchire sichidzawadyanso. Adzakhala mwabata popanda wowaopsa.+

29 “‘“Ndidzawapatsa munda wotchuka+ ndipo sadzafa ndi njala m’dzikomo.+ Mitundu ina ya anthu sidzawanyozanso.+ 30 ‘Iwo adzadziwa kuti ine, Yehova Mulungu wawo, ndili nawo limodzi+ ndiponso kuti iwowo, a nyumba ya Isiraeli ndi anthu anga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’+

31 “‘Koma inu nkhosa zanga,+ nkhosa zimene ndikuzisamalira, ndinu anthu ochokera kufumbi. Ine ndine Mulungu wanu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

35 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kudera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+ 3 Uuze deralo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe dera lamapiri la Seiri,+ ine ndithana nawe. Nditambasula dzanja langa ndi kukukhaulitsa.+ Ndikusandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka.+ 4 Mizinda yako ndidzaisandutsa malo owonongeka ndipo iweyo ndidzakusandutsa bwinja.+ Udzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ 5 chifukwa chakuti unali ndi chidani chosatha+ ndi ana a Isiraeli ndipo unali kuwapha ndi lupanga.+ Unachita zimenezi pa nthawi ya tsoka lawo,+ pamene zolakwa zawo zinafika kumapeto.”’+

6 “‘Chotero pali ine Mulungu wamoyo, mlandu wa magazi udzakutsatira chifukwa ndinakonza zoti magazi ako akhetsedwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ndithudi iwe unadana ndi amene unakhetsa magazi awo, choncho mlandu wa magazi udzakutsatira.+ 7 Dera lamapiri la Seiri ndidzalisandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka.+ Kumeneko sikudzapezeka aliyense wodutsako.+ 8 M’mapirimo ndidzadzazamo anthu ophedwa. M’zitunda zako, m’zigwa zako ndi m’mitsinje yako yonse, mudzadzaza anthu ophedwa ndi lupanga.+ 9 Ndidzakusandutsa malo omwe adzakhale owonongeka mpaka kalekale. M’mizinda yako simudzakhalanso anthu,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

10 “Iwe unanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi mayiko awiri awa zidzakhala zanga ndipo ife tidzatenga mayiko awiri onsewo.’+ Unanena zimenezi ngakhale kuti Yehova anali komweko.+ 11 ‘Chotero pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzachitapo kanthu mogwirizana ndi mkwiyo wako ndi nsanje imene unaisonyeza chifukwa chakuti unali kudana nawo,+ ndipo ndikadzakuweruza, iwo adzandidziwa.+ 12 Iwe udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli.+ Pakuti iwe unanena kuti: “Mapiri aja awonongedwa. Aperekedwa kwa ife kuti akhale chakudya chathu.”+ 13 Anthu inu munalankhula modzitama kwa ine ndi pakamwa panu.+ Munachulukitsa mawu anu ondinyoza+ ndipo ineyo ndinamva mawuwo.’+

14 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa nthawi imene dziko lonse lapansi lizidzasangalala, ine ndidzakusandutsa malo owonongeka. 15 Pakuti unali kusangalala chifukwa chakuti cholowa cha nyumba ya Isiraeli chinawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri ndiponso Edomu yense, mudzasanduka bwinja,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

36 “Koma iwe mwana wa munthu, losera zokhudza mapiri a ku Isiraeli. Unene kuti, ‘Inu mapiri a ku Isiraeli,+ tamverani mawu a Yehova. 2 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pajatu mdani wanu wakunenani kuti,+ ‘Eyaa! Tatenga ngakhale malo okwezeka akalekale+ kukhala athu!’”’+

3 “Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mwakhala bwinja+ ndipo adani anu akulumani kumbali zonse.+ Izi zachitika kuti anthu otsala a mitundu ina akutengeni kuti mukhale awo.+ Anthu akunena za inu ndi pakamwa pawo+ ndipo akukunenerani zoipa.+ 4 Tsopano inu mapiri a ku Isiraeli,+ tamverani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walankhula ndi mapiri, zitunda, mitsinje, zigwa ndi malo owonongedwa amene ndi mabwinja.+ Walankhulanso ndi mizinda yopanda anthu imene anthu otsala a mitundu ina anaitenga kukhala yawo. Anthuwo anakhala moizungulira ndipo amainyoza.+ 5 Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena ndi akuti, ‘Ndithudi, ndidzadzudzula anthu otsala a mitundu ina ndiponso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo. Iwo analitenga akusangalala+ komanso kunyoza mumtima mwawo+ poona kuti atenga dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto.’”’+

6 “Pa chifukwa chimenechi, losera zokhudza dziko la Isiraeli. Lankhula kwa mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ineyo ndidzalankhula ndili waukali ndiponso nditakwiya chifukwa chakuti mitundu ina ya anthu yakhala ikukunyozani.”’+

7 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndalumbira nditakweza dzanja langa+ kuti mitundu imene yakuzungulirani idzakhala yonyozeka.+ 8 Koma inu mapiri a Isiraeli, mudzatulutsa nthambi ndi kubalira zipatso anthu anga Aisiraeli,+ chifukwa chakuti atsala pang’ono kulowa m’dziko lino.+ 9 Ine ndidzatembenukira kwa inu ndi kukuthandizani.+ Inu mapiri a ku Isiraeli, ndithu anthu adzalima minda mwa inu ndi kubzala mbewu.+ 10 Ndidzachulukitsa anthu mwa inu. Ndidzachulukitsa nyumba yonse ya Isiraeli.+ M’mizinda mudzakhala anthu+ ndipo malo owonongeka adzamangidwanso.+ 11 Inde, ndidzachulukitsa anthu ndi nyama+ ndipo adzachulukana ndi kuberekana kwambiri. Ndidzachititsa kuti anthu akhale mwa inu monga momwe zinalili poyamba+ ndipo ndidzakuchitirani zabwino zambiri kuposa poyamba.+ Choncho inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 12 Ndidzachititsa kuti anthu anga Aisiraeli azidzayendayenda mwa inu, ndipo adzakutengani kukhala awo.+ Inu mudzakhala cholowa chawo+ ndipo simudzawapheranso ana.’”+

13 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Anthu akukunenani kuti: “Inu ndinu odya anthu ndipo mwakhala dziko lopha ana a mitundu ya anthu okhala mwa inu.”’+ 14 ‘Pa chifukwa chimenechi inu simudzadyanso anthu+ ndipo simudzaphanso ana a mitundu ya anthu okhala mwa inu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15 ‘Ndidzathetsa nkhani zonyoza zimene anthu a mitundu ina amakunenerani.+ Mitundu ya anthu sidzakunyozaninso+ ndipo simudzakhumudwitsanso mitundu ya anthu okhala mwa inu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

16 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 17 “Iwe mwana wa munthu, pamene a nyumba ya Isiraeli anali kukhala m’dziko lawo, anali kudetsa dzikolo ndi njira zawo komanso zochita zawo.+ Pamaso panga, njira zawo zakhala ngati zonyansa za mkazi amene akusamba.+ 18 Pamenepo ndinawatsanulira mkwiyo wanga chifukwa cha magazi amene iwo anakhetsa m’dziko+ limenenso analidetsa ndi mafano awo onyansa.+ 19 Choncho ndinawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu, moti anamwazikira m’mayiko osiyanasiyana.+ Ndinawaweruza mogwirizana ndi njira zawo komanso zochita zawo.+ 20 Pamenepo iwo anapita kwa anthu a mitundu ina ndipo anthuwo anayamba kudetsa dzina langa loyera+ ponena za iwowo kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, ndipo anachoka m’dziko lake.’+ 21 Ndidzamva chisoni chifukwa cha dzina langa loyera limene nyumba ya Isiraeli yalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene iwo anapita.”+

22 “Chotero uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mwalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+ 23 ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 24 ‘Ndidzakutengani pakati pa anthu a mitundu ina n’kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko onse. Kenako ndidzakubweretsani m’dziko lanu.+ 25 Ine ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera. Ndidzakuyeretsani+ pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+ 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano,+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa inu.+ Ndidzakuchotserani mtima wanu wamwala n’kukupatsani mtima wamnofu.+ 27 Ndidzaika mzimu wanga mwa inu,+ ndipo ndidzakuchititsani kuyenda motsatira malamulo anga.+ Mudzasunga zigamulo zanga ndi kuzitsatira.+ 28 Inu mudzakhala m’dziko limene ndinapatsa makolo anu.+ Mudzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.’+

29 “‘Ndidzakupulumutsani ku zinthu zanu zonse zodetsa,+ ndipo ndidzauza mbewu kuti zibereke kwambiri moti sindidzabweretsanso njala pakati panu.+ 30 Ndidzachulukitsa zipatso za mtengo ndi zokolola zakumunda kuti musadzanyozekenso chifukwa cha njala pakati pa mitundu ina ya anthu.+ 31 Choncho mudzakumbukira njira zanu zoipa ndi zochita zanu zimene sizinali zabwino.+ Mudzanyansidwa ndi zochita zanu, zolakwa zanu ndi zinthu zonyansa zimene munachita.+ 32 Dziwani kuti ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Inu a nyumba ya Isiraeli, chitani manyazi ndi kuona kuti mwanyozeka chifukwa cha njira zanu.’+

33 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limene ndidzakuyeretseni kuchotsa zolakwa zanu zonse, ndidzachititsanso kuti m’mizinda yanu mukhale anthu+ ndipo malo owonongeka adzamangidwanso.+ 34 Anthu adzalima m’dziko limene linali lowonongedwa. Adzalima m’dziko limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja.+ 35 Anthu adzanena kuti: “Dziko ilo limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.+ Mizinda imene inawonongedwa ija, imene inali mabwinja ndiponso imene nyumba zake zinagwetsedwa, tsopano ili ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo mukukhala anthu.”+ 36 Anthu a mitundu ina okuzungulirani amene adzatsale, adzadziwa kuti ine Yehova, ndamanga zinthu zimene zinagwetsedwa.+ Adzadziwa kuti ndabzala mitengo m’dziko limene linali bwinja. Ine Yehova ndanena zimenezi ndipo ndazichita.’+

37 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzalola kuti a nyumba ya Isiraeli andipemphe zoti ndiwachitire,+ ndipo ndidzachulukitsa anthu awo ngati gulu la nkhosa.+ 38 Mizinda imene inali mabwinja idzadzaza anthu ochuluka ngati khamu la oyera,+ ndiponso ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa nthawi za zikondwerero,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

37 Dzanja la Yehova linali pa ine+ moti mzimu wa Yehova unanditenga+ ndi kukandikhazika m’chigwa mmene munali mafupa okhaokha.+ 2 Iye anandiyendetsa m’chigwamo kuti ndione mafupa onsewo. Ndinaona kuti m’chigwamo munali mafupa ambiri ndipo anali ouma kwambiri.+ 3 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa awa angakhale ndi moyo?” Pamenepo ndinayankha kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu amene mukudziwa bwino zimenezo.”+ 4 Ndiyeno anandiuza kuti: “Losera zokhudza mafupa amenewa ndipo uwauze kuti, ‘Inu mafupa ouma, imvani mawu a Yehova:

5 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mafupa awa kuti: “Ndiika mpweya mwa inu ndipo mukhala amoyo.+ 6 Ndidzakuikirani mitsempha ndi kukupatsani mnofu. Ndidzakukutani ndi khungu ndi kuika mpweya mwa inu ndipo mudzakhala ndi moyo.+ Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+

7 Ine ndinalosera mmene anandiuzira.+ Pamene ndinali kulosera, panayamba kumveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede! Pa nthawiyo mafupawo anali kubwera pamodzi n’kumalumikizana. 8 Kenako ndinangoona mitsempha ndi mnofu zitakuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake. Koma m’mafupawo munalibe mpweya.

9 Tsopano anandiuza kuti: “Losera kwa mphepo. Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uuze mphepoyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mphepo! Bwera kuchokera kumbali zonse zinayi ndi kuwomba anthu ophedwawa+ kuti akhalenso ndi moyo.”’”+

10 Pamenepo ndinalosera monga mmene anandiuzira ndipo mpweya unalowa mwa anthuwo. Iwo anakhala ndi moyo ndipo anaimirira.+ Anali khamu lalikulu la gulu lankhondo.

11 Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, mafupawa akuimira nyumba yonse ya Isiraeli.+ Iwo akunena kuti, ‘Mafupa athu auma ndipo tilibenso chiyembekezo chilichonse.+ Atilekanitsa ndi anzathu ndipo tili kwatokhatokha.’ 12 Choncho losera, uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatsegula manda anu,+ inu anthu anga, ndipo ndidzakutulutsani m’mandamo ndi kukubweretsani m’dziko la Isiraeli.+ 13 Inu anthu anga, ine ndikadzatsegula manda anu n’kukutulutsani m’mandamo, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’+ 14 ‘Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhala amoyo.+ Ndidzakukhazikani m’dziko lanu ndipo mudzadziwa kuti ine Yehova ndinanena zimenezi ndipo ndazichita,’ watero Yehova.”+

15 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 16 “Koma iwe mwana wa munthu, tenga ndodo+ ndi kulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi anzake, ana a Isiraeli.’+ Utengenso ndodo ina ndi kulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu+ komanso anzawo onse a nyumba ya Isiraeli.’+ 17 Ndiyeno uziike pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi. Chotero ndodozo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja lako.+ 18 Anthu a mtundu wako akayamba kukufunsa kuti, ‘Kodi sutiuza kuti zinthu izi zikutanthauza chiyani?’+ 19 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ndodo ya Yosefe imene ili m’dzanja la Efuraimu. Ndodo imeneyi ikuimiranso mafuko a Isiraeli omwe ndi anzake a Efuraimu. Ndidzaika mafukowo pandodo ya Yuda ndipo ndodo ziwirizo zidzakhala ndodo imodzi.+ Ndodozo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja langa.”’ 20 Ndodo zimene wazilembazo zikhale m’dzanja lako pamaso pawo.+

21 “Uwauzenso kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ana a Isiraeli kuchokera pakati pa mitundu ina ya anthu kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko owazungulira ndipo ndidzawabweretsa m’dziko lawo.+ 22 Ndidzawaphatikiza kuti akhale mtundu umodzi m’dzikolo,+ m’mapiri a Isiraeli. Onsewo adzakhala ndi mfumu imodzi+ ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawanika kukhala maufumu awiri.+ 23 Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa, zinthu zawo zonyansa ndi zochita zawo zonse zophwanya malamulo.+ Ndidzawapulumutsa ku machimo onse amene anali kuchita m’malo awo okhala, ndipo ndidzawayeretsa.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+

24 “‘“Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo.+ Onse adzakhala ndi m’busa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga+ ndipo adzasunga malamulo anga+ ndi kuwatsatira.+ 25 Anthu amenewa adzakhala m’dziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu anakhalamo.+ Adzakhala m’dzikomo+ pamodzi ndi ana awo ndiponso zidzukulu zawo mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wawo mpaka kalekale.+

26 “‘“Ndidzachita nawo pangano la mtendere,+ moti adzakhala m’pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.+ Ine ndidzawakhazikitsa m’dzikolo, ndidzawachulukitsa+ ndipo ndidzakhazikitsa malo anga opatulika pakati pawo mpaka kalekale.+ 27 Iwo adzakhala muhema wanga.+ Ine ndidzakhaladi Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.+ 28 Malo anga opatulika akadzakhala pakati pawo mpaka kalekale, mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine Yehova+ ndikuyeretsa Isiraeli.”’”+

38 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu,+ yang’ana Gogi wa kudziko la Magogi,+ mtsogoleri wamkulu wa Meseke+ ndi Tubala,+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzam’chitikire. 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndithana nawe iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu wa Meseke ndi Tubala. 4 Ndithu ine ndidzakubweza n’kukukola chibwano ndi ngowe.+ Kenako ndidzakukokera pafupi limodzi ndi gulu lako lonse lankhondo,+ mahatchi ako ndi asilikali ako okwera pamahatchi. Asilikali onsewa ndi ovala mwaulemerero.+ Iwo ndi khamu lalikulu lonyamula zishango zazikulu ndi zazing’ono, ndipo onsewo ndi aluso lomenya nkhondo pogwiritsa ntchito malupanga.+ 5 Udzabwera pamodzi ndi asilikali a ku Perisiya,+ Itiyopiya+ ndi Puti.+ Onsewa adzanyamula zishango zazing’ono ndipo adzavala zisoti. 6 Udzabweranso ndi Gomeri+ ndi magulu ake onse a asilikali, komanso ndi ana a Togarima+ ochokera kumadera akutali kwambiri a kumpoto. Iwo adzabwera ndi magulu awo onse a asilikali. Chotero iwe udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu.+

7 “‘“Konzeka, iwe ndi khamu lako lonse+ limene lasonkhana kwa iwe. Nonse mukhale okonzeka ndipo iwe ukhale mtsogoleri wawo.

8 “‘“Pakapita masiku ambiri, ine ndidzatembenukira kwa iwe. Pakatha zaka zambiri, iwe udzapita kudziko+ la anthu amene anapulumutsidwa ku lupanga ndi kubwerera kwawo. Udzapita kudziko la anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina ya anthu+ n’kukakhala kumapiri a ku Isiraeli. Dziko lawo linali kuwonongedwa nthawi zonse ndipo tsopano muli anthu amene anachokera m’mayiko a anthu a mitundu ina. Onsewo akukhala m’dzikoli mwabata.+ 9 Iwe udzabwera m’dzikolo ngati mphepo yamkuntho.+ Iweyo, magulu ako onse a asilikali, pamodzi ndi anthu ambiri a mitundu ina, mudzaphimba dzikolo ngati mitambo.”’+

10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsikulo maganizo adzakubwerera mumtima mwako+ ndipo udzaganiza zochita chiwembu choipa kwambiri.+ 11 Udzanena kuti: “Ndipita kukaukira dziko lokhala ndi midzi yopanda mipanda.+ Ndipita kukaukira anthu amene akukhala mwabata, popanda chowasokoneza. Ndikaukira anthu onsewo amene akukhala m’midzi yopanda mipanda+ ndipo alibe zotsekera ndiponso zitseko.” 12 Udzapita kumeneko kuti ukalande+ ndi kutengako zinthu zambiri, ndiponso kuti ukaukire dziko lowonongedwa limene tsopano mukukhala anthu.+ Udzapita kukaukira anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina,+ amene akusonkhanitsa chuma ndi katundu,+ komanso amene akukhala pakatikati+ pa dziko lapansi.

13 “‘Sheba,+ Dedani,+ amalonda a ku Tarisi+ ndi mikango yawo yonse yamphamvu+ adzakufunsa kuti: “Kodi wasonkhanitsa khamu lako kuti udzalande zinthu zambiri? Kodi ukufuna kudzatenga siliva, golide, chuma ndi katundu?”’

14 “Chotero losera, iwe mwana wa munthu, ndipo uuze Gogi kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Anthu anga Aisiraeli akamadzakhala mwabata, ndithu iwe udzadziwa zimenezo.+ 15 Udzabwera kuchokera kumalo ako, kumadera akutali a kumpoto.+ Udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala chigulu chachikulu chankhondo. Onsewo adzabwera atakwera pamahatchi.+ 16 Ndithu iwe udzabwera ngati mitambo kudzaphimba dzikolo ndi kudzaukira anthu anga Aisiraeli.+ Zimenezi zidzachitika m’masiku otsiriza, ndipo ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa.+ Ndidzachita izi kuti anthu a mitundu ina adzandidziwe pamene ndidzadziyeretse pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.”’+

17 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Kodi iwe ndiwe+ yemwe uja amene ndinkakunena kale kudzera mwa atumiki anga, aneneri a Isiraeli? Aneneriwo ankalosera chaka ndi chaka m’masiku amenewo kuti ndidzakutumiza kwa iwo kuti ukawaukire.’+

18 “‘Pa tsiku limenelo, tsiku limene Gogi adzabwere m’dziko la Isiraeli, mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno mwanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 19 ‘Ine ndidzalankhula mwaukali wanga+ woyaka moto komanso nditakwiya kwambiri.+ Ndithudi, pa tsikulo m’dziko la Isiraeli mudzachitika chivomezi chachikulu.+ 20 Chifukwa cha ine, nsomba zam’nyanja, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga, zilombo zakutchire, zokwawa zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse amene ali padziko lapansi, adzanjenjemera.+ Mapiri adzagwetsedwa,+ misewu yotsetsereka idzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.’

21 “‘Ndidzamubweretsera lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.+ 22 Ine ndidzamuweruza+ ndi mliri+ ndiponso magazi.+ Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala,+ moto+ ndi sulufule. Ndidzagwetsa zimenezi pa iyeyo, pagulu lake la asilikali ndi pa mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.+ 23 Ndidzadzilemekeza, kudziyeretsa+ ndi kuchititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

39 “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire Gogi.+ Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndithana nawe iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu wa Meseke+ ndi Tubala.+ 2 Ndidzakubweza ndi kukutsogolera.+ Ndidzakutenga kuchokera kumadera akutali kwambiri a kumpoto,+ n’kukubweretsa kumapiri a ku Isiraeli. 3 Ndidzakuphumitsa uta m’dzanja lako lamanzere, ndipo ndidzachititsa kuti mivi yako igwe pansi kuchoka m’dzanja lako lamanja. 4 Iwe udzafera m’mapiri a ku Isiraeli+ limodzi ndi magulu ako onse a asilikali ndi anthu a mitundu ina amene adzakhale nawe. Ndidzakuperekani kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.”’+

5 “‘Iweyo udzagwera panthaka,+ pakuti ine ndanena zimenezi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

6 “‘Ndidzatumiza moto ku Magogi+ ndi kwa anthu amene akukhala mwabata m’zilumba,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 7 Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Aisiraeli. Sindidzalolanso kuti dzina langa lidetsedwe,+ ndipo mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ Woyera wa ku Isiraeli.’+

8 “‘Tamvera! Zimene ulosiwu ukunena zidzachitika ndipo zidzakwaniritsidwa,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ine ndakhala ndikunena za tsiku limenelo.+ 9 Anthu okhala m’mizinda ya Isiraeli adzakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondo. Zida zake ndizo zishango zazing’ono, zishango zazikulu, mauta, mivi, zobayira ndi mikondo ing’onoing’ono. Adzakoleza moto+ pogwiritsa ntchito zida zimenezi kwa zaka 7. 10 Iwo sadzanyamula mitengo kutchire kapena kutola nkhuni kunkhalango, chifukwa chakuti adzakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondozo.’

“‘Adzalanda zinthu za anthu amene anali kuwalanda zinthu zawo,+ ndipo adzatenga katundu wa anthu amene anali kutenga katundu wawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

11 “‘Pa tsiku limenelo Gogi+ ndidzam’patsa malo kuti akhale manda ake mu Isiraeli. Ndidzam’patsa chigwa cha kum’mawa kwa nyanja, chomwe ndi chigwa cha anthu ongodutsa. Chigwacho chidzatseka njira ya anthu ongodutsawo. Kumeneko iwo adzaika m’manda Gogi pamodzi ndi khamu lake lonse, ndipo adzatcha chigwacho kuti Chigwa cha Khamu la Gogi.+ 12 Kwa miyezi 7, a nyumba ya Isiraeli adzakhala akuika m’manda Gogi ndi khamu lake kuti ayeretse dzikolo.+ 13 Anthu onse a m’dzikolo adzagwira ntchito yofotsera mitembo. Iwo adzatchuka chifukwa cha ntchito imeneyi pa tsiku limene ine ndidzalemekezeke,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

14 “‘Padzakhala amuna amene azidzagwira ntchito nthawi zonse. Iwo azidzayenda m’dzikolo n’kumafotsera mitembo pamodzi ndi anthu ongodutsa. Amenewa azidzakwirira mitembo yotsalira pamtunda. Adzachita zimenezi kuti ayeretse dziko lapansi. Iwo adzakhala akufunafuna mitembo kwa miyezi 7. 15 Anthu ongodutsa akamadzadutsa m’dzikolo, wina n’kuona fupa la munthu, azidzaikapo chizindikiro mpaka anthu ofotsera aja atakafotsera fupalo m’Chigwa cha Khamu la Gogi.+ 16 Kumeneko kudzakhala mzinda wotchedwanso Hamona, ndipo anthu adzayeretsa dzikolo.’+

17 “Koma kwa iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Uza mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zonse zakutchire+ kuti: “Sonkhanani mubwere kuno. Sonkhanani pamodzi kuzungulira nsembe yanga imene ndikukuperekerani. Imeneyi ndi nsembe yaikulu m’mapiri a ku Isiraeli.+ Mukabwera mudzadya nyama ndi kumwa magazi.+ 18 Mudzadya mnofu wa anthu amphamvu,+ mudzamwa magazi a atsogoleri a dziko lapansi, nkhosa zamphongo, ana a nkhosa amphongo,+ mbuzi zamphongo ndi ng’ombe zamphongo.+ Zonsezi ndi nyama zonenepa za ku Basana.+ 19 Inu mudzadya mafuta ndi kukhuta,+ ndipo mudzamwa magazi mpaka kuledzera nawo. Zimenezi zidzachokera pa nsembe yanga imene ndidzakuperekereni.”’

20 “‘Inu mudzakhuta patebulo langa. Mudzadya nyama ya mahatchi, ya okwera magaleta, ya anthu amphamvu ndi ankhondo a mitundu yosiyanasiyana,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

21 “‘Ndidzasonyeza ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu. Mitundu yonse ya anthu idzaona chiweruzo chimene ndidzapereke+ ndiponso mphamvu za dzanja langa.+ 22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo, a nyumba ya Isiraeli adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Mulungu wawo.+ 23 Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Adzadziwa kuti anali kundichitira zinthu zosakhulupirika. N’chifukwa chake ine ndinawabisira nkhope yanga+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo ndipo onsewo anaphedwa ndi lupanga.+ 24 Ndinawachitira zinthu mogwirizana ndi zonyansa zimene anachita komanso chifukwa chakuti anaphwanya malamulo,+ moti ndinawabisira nkhope yanga.’

25 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsopano ndibweretsa ana a Yakobo omwe anatengedwa kupita kumayiko ena,+ ndipo ndichitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Nditeteza dzina langa loyera kuti lisadetsedwe.*+ 26 Akadzakhala m’dziko lawo mwabata+ popanda wowaopsa,+ adzakhala atachita manyazi mokwanira+ chifukwa cha zinthu zonse zosakhulupirika zimene anandichitira.+ 27 Ndikadzawabweretsa kuchokera ku mitundu ina ya anthu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko a adani awo,+ ndidzadziyeretsa pakati pawo pamaso pa mitundu yambiri ya anthu.’+

28 “‘Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndikadzawapititsa kumayiko ena n’kuwabwezanso kudziko lawo onse pamodzi.+ Kumayikowo ndidzatengako Aisiraeli onse moti sindidzasiyako aliyense.+ 29 Sindidzawabisiranso nkhope yanga+ chifukwa panyumba ya Isiraeli, ndidzatsanulirapo mzimu wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

40 M’chaka cha 25 kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo,+ kuchiyambi kwa chakacho, pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, m’chaka cha 14 kuchokera pamene mzinda unawonongedwa,+ pa tsiku limeneli dzanja la Yehova linandikhudza,+ ndipo iye ananditengera kumalo enaake.+ 2 M’masomphenya a Mulungu, iye ananditengera m’dziko la Isiraeli ndi kundikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali ya kum’mwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.+

3 Kenako ananditengera kumeneko ndipo ndinaonako munthu wamwamuna. Munthuyo anali kuoneka wonyezimira ngati mkuwa.+ M’manja mwake munali chingwe cha fulakesi* ndi bango loyezera,+ ndipo anaima pachipata. 4 Tsopano munthuyo anayamba kulankhula nane kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ ona ndi maso ako, imva ndi makutu ako, ndipo uike mtima wako pa zonse zimene ndikuonetse, chifukwa wabweretsedwa kuno kuti ine ndikuonetse zinthu zimenezi. Ukauze nyumba ya Isiraeli zonse zimene uone kuno.”+

5 Ndiyeno ndinaona kuti panali nyumba yomwe inali ndi mpanda wozungulira nyumba yonseyo. M’manja mwa munthu uja munali bango loyezera. Bangolo linali lalitali kukwana mikono* 6 potengera muyezo wa mkono ndi chikhatho. Tsopano munthuyo anayamba kuyeza mpandawo, ndipo anapeza kuti unali wochindikala bango limodzi komanso kuchokera pansi kupita m’mwamba unali wautali bango limodzi.

6 Kenako anafika pachipata chimene chinayang’ana kum’mawa+ ndipo anakwera pamasitepe ake. Pamenepo iye anayamba kuyeza malo apafupi ndi khomo la kanyumba ka pachipatako+ ndipo anapeza kuti malowo anali bango limodzi m’lifupi. Malo apafupi ndi khomo la mbali ina ya kanyumbako analinso bango limodzi m’lifupi mwake. 7 Chipinda cha alonda chinali bango limodzi m’litali ndi bango limodzi m’lifupi. Kuchokera pachipinda cha alonda kukafika pachipinda china cha alonda+ panali mikono isanu. Malo apafupi ndi khomo la kanyumbako, pafupi ndi khonde lamkati anali bango limodzi.

8 Ndiyeno anayeza khonde la kanyumbako loyang’ana kubwalo lakunja, ndipo anapeza kuti linali bango limodzi.+ 9 Anayeza khonde la kanyumba ka pachipata n’kupeza kuti linali mikono 8. Zipilala zake zam’mbali zinali mikono iwiri. Khonde la kanyumbako linali loyang’ana kubwalo lakunja.

10 Zipinda za alonda za pachipata cha kum’mawa zinalipo zitatu mbali iyi ndi zitatu mbali inayo. Miyezo ya zipinda zitatuzo inali yofanana, ndipo zipilala zam’mbali zinalinso zofanana, mbali iyi ndi mbali inayo.

11 Kenako anayeza m’lifupi mwa malo apafupi ndi khomo la kanyumba ka pachipata n’kupeza mikono 10. Anayezanso m’litali mwa chipata n’kupeza mikono 13.

12 Malo otchinga ndi mpanda, kutsogolo kwa zipinda za alonda, anali mkono umodzi. Kumbali zonse kunali malo otchinga ndi mpanda okwana mkono umodzi. Chipinda chilichonse cha alonda chinali mikono 6 mbali iyi ndiponso mikono 6 mbali inayo.

13 Iye anapitiriza kuyeza kanyumba ka pachipatako kuchokera padenga* la chipinda chimodzi cha alonda kukafika padenga la chipinda china cha alonda ndipo anapeza mikono 25.+ Khomo la chipinda cha alonda cha mbali iyi linali moyang’anizana ndi khomo la chipinda cha mbali inayo. 14 Kenako anayeza zipilala zam’mbali ndipo anapeza kuti zinali zazitali mikono 60 kuchokera pansi kupita m’mwamba. Zipilala zam’mbalizo zinali zoyang’ana kubwalo, m’zipata zonse. 15 Kuchokera kutsogolo kwa khomo lakunja la kanyumba ka pachipata, kukafika kutsogolo kwa khonde limene linali kukhomo lamkati la kanyumbako, panali mikono 50.

16 Zipinda za alondazo komanso zipilala zimene zinali m’mbali mwa zipindazo zinali ndi mawindo okhala ndi mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja+ kuzungulira kanyumba konseko. Umu ndi mmenenso zinalili ndi mawindo apakhonde. Mkati mwa kanyumbako munali mawindo aakulu mkati, kuzungulira mbali zonse ndipo pazipilala zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.+

17 Kenako anandipititsa kubwalo lakunja. Kumeneko ndinaona zipinda zodyeramo+ ndipo pansi pa bwalo lonselo panali powaka miyala. Pabwalo lowaka miyalalo panali zipinda zodyeramo zokwana 30.+ 18 M’lifupi mwa malo owaka miyala am’mbali mwa tinyumba ta zipata munali mofanana ndendende ndi m’litali mwa tinyumbato. Amenewa anali malo owaka miyala a m’munsi.

19 Munthu uja anapitiriza kuyeza kuchokera kutsogolo kwa kanyumba ka pachipata cha m’munsi kukafika kutsogolo kwa bwalo lamkati. Malo amenewa anali mikono 100, kum’mawa ndi kumpoto.

20 Bwalo lakunja linali ndi kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kumpoto. Iye anayeza m’litali ndi m’lifupi mwake. 21 Zipinda zake za alonda zinali zitatu mbali iyi ndiponso zitatu mbali inayo. Miyezo ya zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake, inali yofanana ndi miyezo ya kanyumba ka pachipata choyamba chija. M’litali mwake kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 22 Miyezo ya mawindo ake, khonde lake ndi zithunzi zake za mtengo wa kanjedza,+ inali yofanana ndi miyezo ya zinthu zomwezi za kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mawa. Anthu akafuna kulowa m’kanyumbako anali kukwera masitepe 7, ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa anthuwo.

23 Chipata cha bwalo lamkati chinayang’anizana ndi chipata cha kumpoto. Chipata cha kum’mawa cha bwalo lamkati nachonso chinayang’anizana ndi chipata cha kum’mawa. Munthu uja anayezanso mikono 100 kuchokera pachipata kukafika pachipata china.

24 Kenako ananditengera kumbali ya kum’mwera. Kumeneko ndinaonakonso kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mwera.+ Iye anayeza zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake ndipo miyezo yake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba ta zipata zina zija. 25 Kanyumba ka pachipata kameneka ndi khonde lake zinali ndi mawindo ofanana ndi a tinyumba ta zipata zina zija kuzungulira kanyumbako. M’litali, kanyumbako kanali mikono 50 ndipo m’lifupi kanali mikono 25. 26 Kanyumba kameneka kanali ndi masitepe 7 okwerera m’chipatacho,+ ndipo kutsogolo kwawo kunali khonde. Pazipilala zimene zinali m’mbali mwa khondelo, chimodzi mbali iyi ndi china mbali inayo, panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.

27 Bwalo lamkati linali ndi chipata kumbali ya kum’mwera. Ndipo iye anayeza kuchokera pachipata kulowera kum’mwera kukafika pachipata china. Mtunda umenewo unakwana mikono 100. 28 Kenako ananditengera m’bwalo lamkati kudzera pachipata cha kum’mwera. Munthu uja anayeza kanyumba ka pachipata cha kum’mwera ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 29 Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba ka pachipatako, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kanyumba ka pachipata konseko ndi khonde lake zinali ndi mawindo. M’litali mwake kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25.+ 30 Tinyumba tonse ta zipata zolowera m’bwalo lamkati tinali ndi khonde. M’litali mwake khondelo linali mikono 25 ndipo m’lifupi linali mikono isanu. 31 Khonde lake linayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zake zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza+ ndipo masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8.+

32 Kenako ananditengera m’bwalo lamkati kudzera mbali ya kum’mawa. Kumeneko iye anayeza kanyumba ka pachipatako ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 33 Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba ka pachipatako, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kanyumba ka pachipata konseko ndi khonde lake zinali ndi mawindo. M’litali mwake, kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 34 Khonde lake linayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zake zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndi kumbali inayo, ndipo masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8.

35 Kenako ananditengera kuchipata cha kumpoto.+ Kumeneko iye anayeza kanyumba ka pachipatako ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija.+ 36 Iye anayeza zipinda za alonda, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake. Kanyumba ka pachipata konseko kanali ndi mawindo. M’litali mwake, kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 37 Zipilala zake zam’mbali zinayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zam’mbalizo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndi kumbali inayo.+ Masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8.

38 Pafupi ndi zipilala zam’mbali mwa tinyumba ta zipatazo panali chipinda chodyeramo. Kumeneko n’kumene anali kutsukira nsembe yopsereza yathunthu.+

39 Pakhonde la kanyumba ka pachipatako panali matebulo awiri kumbali iyi ndi matebulo ena awiri kumbali inayo. Pamatebulowo anali kupherapo nsembe yopsereza yathunthu,+ nsembe yamachimo+ ndi nsembe ya kupalamula.+ 40 Kunja kwa kanyumba ka pachipata cha mbali ya kumpoto, kukhomo lolowera m’kanyumbako, kunali matebulo awiri. Kumbali inayo, pafupi ndi khonde la kanyumbako, kunalinso matebulo awiri. 41 Kunja kwa kanyumba ka pachipatako kunali matebulo anayi ndipo mkati mwa kanyumbako munalinso matebulo anayi. Matebulo onse amene anali kupherapo nyama analipo 8. 42 Matebulo anayi a nsembe zopsereza zathunthuwo anali amiyala yosema. M’litali mwake anali mkono umodzi ndi hafu, m’lifupi mwake anali mkono umodzi ndi hafu ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba anali aatali mkono umodzi. Pamatebulo amenewa analinso kuikapo zida zophera nyama ya nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina. 43 Mashelefu oikamo katundu anali chikhatho chimodzi m’lifupi mwawo. Mashelefuwo anawaika kuzungulira khoma lonse lamkati ndipo anawalimbitsa kwambiri. Pamatebulo aja anali kuikapo nyama ya nsembe yoperekedwa monga mphatso.+

44 Kunja kwa kanyumba ka pachipata chamkati kunali zipinda zodyeramo oimba.+ Zipinda zimenezi zinali m’bwalo lamkati kumbali ya chipata cha kumpoto. Zipindazo zinayang’ana kum’mwera. Chipinda chimodzi chinali mbali ya kuchipata cha kum’mawa, ndipo chinayang’ana kumpoto.

45 Pamenepo munthu uja anandiuza kuti: “Chipinda chodyeramo ichi, chimene chayang’ana kum’mwera, ndi cha ansembe amene akutumikira panyumbayi.+ 46 Chipinda chodyeramo chimene chayang’ana kumpoto ndi cha ansembe ogwira ntchito paguwa lansembe,+ omwe ndi ana a Zadoki.+ Iwo ndi ochokera mwa ana a Levi ndipo amayandikira Yehova ndi kum’tumikira.”+

47 Munthu uja anayezanso bwalo lamkati. Iye anapeza kuti m’litali mwake, linali mikono 100 ndipo m’lifupi linalinso mikono 100. Bwalolo linali lofanana mbali zonse zinayi. Kutsogolo kwa nyumbayo kunali guwa lansembe.

48 Kenako ananditengera pakhonde la nyumbayo.+ Pamenepo anayeza chipilala cham’mbali cha khondelo ndipo anapeza kuti chinali mikono isanu mbali iyi ndi mikono isanu mbali inayo. M’lifupi mwa khomo la nyumbayo munali mikono itatu mbali iyi ndi mikono itatu mbali inayo.

49 Khonde la nyumbayo linali mikono 20 m’litali mwake ndi mikono 11 m’lifupi. Kuti munthu afike pakhondepo anali kukwera masitepe. Pafupi ndi zipilala zam’mbalizo panali nsanamira, imodzi mbali iyi, ina mbali inayo.+

41 Ndiyeno munthu uja ananditengera m’kachisi.* Mmenemo anayamba kuyeza zipilala zam’mbali. Chipilala china chinali mbali ya kumanzere ndipo china mbali ya kudzanja lamanja. Chipilala chilichonse chinali mikono 6 m’lifupi. Umenewu ndiwo unali muyezo wa chipilala chilichonse m’lifupi mwake. 2 Khomo lolowera m’chipinda chakunja linali lalikulu mikono 10, ndipo kuchokera pakhomolo kukafika pakona panali khoma la mikono isanu mbali iyi, ndi mikono isanu mbali inayo. Anayezanso m’litali mwa chipinda chakunja ndipo chinali mikono 40, m’lifupi mwake chinali mikono 20.

3 Kenako analowa m’chipinda chamkati n’kuyamba kuyeza chipilala cham’mbali cha pakhomo ndipo anapeza kuti kuchindikala kwake chinali mikono iwiri. Anayezanso kukula kwa khomo ndipo anapeza kuti linali mikono 6. Kuchokera pakhomo kukafika pakona panali mikono 7. 4 Ndiyeno anayeza makoma a chipinda chamkati kumbuyo kwa kachisi, ndipo anapeza kuti anali mikono 20 m’litali ndi mikono 20 m’lifupi.+ Kenako anandiuza kuti: “Amenewa ndi Malo Oyera Koposa.”+

5 Anayezanso kuchindikala kwa khoma la nyumbayo ndipo anapeza kuti linali mikono 6. M’lifupi mwa chipinda cham’mbali munali mikono inayi. Umu ndi mmene zinalili kuzungulira nyumba yonseyo.+ 6 M’mbali mwa nyumbayo munali mizere itatu ya zipinda zosanjikizana. Mzere uliwonse unali ndi zipinda 30. Zipinda zam’mbali kuzungulira nyumbayo zinali kulowa ku khoma la nyumbayo kuti zikhale ndi chozichirikiza. Koma sizinachirikizike ndi khoma la nyumbayo.+ 7 Zipinda za mzere wachiwiri zinali zokulirapo m’mbali kuposa za mzere woyamba, ndipo zipinda za mzere wachitatu zinali zokulirapo m’mbali kuposa za mzere wachiwiri. Panali masitepe oyenda chozungulira opitira m’zipinda zam’mwamba.+ Choncho zipinda za mzere wachitatu zinali zokulirapo kuposa zipinda za mzere wachiwiri, ndipo zipinda za mzere wachiwiri zinali zokulirapo kuposa za mzere woyamba. Munthu akafuna kupita kuzipinda zam’mwamba kuchokera kuzipinda zapansi+ anali kudutsa m’zipinda zapakati.

8 Ndinaona kuti nyumba yonseyo anaimanga pamaziko aatali omwe anachita khonde kuzungulira nyumbayo. Kutalika kwa maziko a zipinda zam’mbali kunali bango lathunthu, lalitali mikono 6 kuchokera pansi kukafika polumikizira.+ 9 Khoma lakunja la chipinda cham’mbali linali lochindikala mikono isanu. Pomanga zipinda zam’mbali za nyumbayo, anasiya mpata m’mphepete mwa nyumbayo.

10 Kuchokera pazipinda zodyera+ kukafika pamaziko a nyumbayo panali mikono 20 kumbali zonse za nyumbayo. 11 Makomo a zipinda zam’mbali analoza kumpata wa m’mphepete mwa nyumbayo. Khomo limodzi linayang’ana kumpoto lina linayang’ana kum’mwera. Mpata wa m’mphepete mwa nyumbayo unali mikono isanu m’lifupi, kumbali zonse za nyumbayo.

12 Kumadzulo kwa nyumbayo kunalinso nyumba ina. Nyumba imeneyo inali mikono 70 m’lifupi mwake. Khoma lonse la nyumbayo linali lochindikala mikono isanu, ndipo m’litali mwake linali mikono 90. Pakati pa nyumba ziwirizi panali mpata waukulu.

13 Munthu uja anayeza kachisi n’kupeza kuti anali mikono 100 m’litali mwake. Anayezanso mpata waukulu umene unali mbali zonse za kachisiyo, nyumba imene inali kumadzulo kwake ndi makoma ake, ndipo zonse pamodzi zinali mikono 100 m’litali. 14 Kenako anayeza kumaso kwa kachisi m’lifupi mwake limodzi ndi mpata waukulu wa mbali ya kum’mawa kwa kachisiyo, ndipo anapeza kuti zinali mikono 100.

15 Munthu uja anayezanso m’litali mwa nyumba ya kumadzulo ija imene inayang’anizana ndi mpata waukulu. Anayeza timakonde take mbali iyi ndi mbali inayo n’kupeza kuti nyumbayo ndi timakondeto zinali mikono 100.

Anayezanso kachisi, malo ake amkati+ ndi makonde oyang’ana kubwalo. 16 Malo atatu onsewa anali ndi mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja.+ Analinso ndi timakonde ndiponso malo a pakhomo. M’makoma onse a kutsogolo kwa malo a pakhomo anakhomamo matabwa+ kuchokera pansi kufika m’mawindo, ndipo mawindowo anali otchinga. 17 Chilichonse panyumbayo chinali ndi muyezo wake. Izi zinali choncho kuyambira pamwamba pa khomo, mkati ndi kunja kwa nyumbayo, khoma lonse kuzungulira mkati mwa nyumbayo ndiponso kunja kwake. 18 Ngakhalenso zithunzi zojambula mochita kugoba za akerubi+ ndi za mitengo ya kanjedza,+ zinali ndi miyezo yake. Mitengoyo inali pakati pa kerubi ndi kerubi mnzake, ndipo akerubiwo anali ndi nkhope ziwiriziwiri.+ 19 Nkhope ya munthu inayang’ana chithunzi cha mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndipo nkhope ya mkango wamphamvu inayang’ana mtengo wa kanjedza kumbali inayo.+ Zithunzi zimenezi zinali zojambula pakhoma mochita kugoba ndipo zinajambulidwa kuzungulira m’nyumba monsemo. 20 Pakhoma la kachisiyo, kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo, anajambulapo mochita kugoba zithunzi za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza.

21 Felemu la pakhomo la kachisi linali lofanana mbali zonse,+ ndipo kutsogolo kwa malo oyera kunali kuoneka motere: 22 Kunali guwa lansembe lamatabwa lalitali mikono itatu kuchokera pansi kufika pamwamba. M’litali mwake munali mikono iwiri ndipo m’makona ake munali mwa matabwa.+ M’litali mwa guwalo ndi m’mbali mwake munali mwa matabwa. Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Ili ndi tebulo limene lili pamaso pa Yehova.”+

23 Pakhomo la kachisi komanso la malo oyera panali zitseko ziwiri.+ 24 Pakhomo lililonse panali zitseko ziwiri. Zitseko zonsezo zinali zotheka kuzitsegula. Khomo limodzi linali ndi zitseko ziwiri ndipo khomo linalo linalinso ndi zitseko ziwiri. 25 Pazitseko za kachisi anajambulapo zithunzi za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza mochita kugoba.+ Zithunzi zimenezi zinali zofanana ndi zimene anajambula m’makoma. Kutsogolo kwa denga la khonde anakhomako mzere wa matabwa otulukira kunja. 26 M’mbali mwa khoma la pakhonde, m’zipinda zam’mbali za nyumbayo ndi pamzere wa matabwawo, munali mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja,+ ndipo anajambulamo zithunzi za mtengo wa kanjedza mbali zonse. Zithunzizi anazijambula mochita kugoba.

42 Munthu uja ananditengera+ kubwalo lakunja kudzera mbali ya kumpoto.+ Kumeneko anandipititsa kumdadada wa zipinda zodyeramo+ zimene zinali kutsogolo kwa mpata waukulu,+ ndiponso kumpoto kwa nyumba imene inali kumadzulo. 2 Kuchokera pakhomo la mbali ya kumpoto, khoma la kutsogolo kwa nyumba zodyeramo linali mikono 100 m’litali ndi mikono 50 m’lifupi. 3 Kuchokera pampata waukulu wa mikono 20 umene unali m’bwalo lamkati+ kukafika pamalo owaka miyala+ amene anali m’bwalo lakunja, panali nyumba ziwiri zoyang’anizana, zomwe zinali ndi zipinda zodyeramo. Nyumbazo zinali ndi mizere itatu ya zipinda zosanjikizana ndipo zipindazo zinali ndi makonde.+ 4 Pakati pa zipinda zodyeramo panali njira yolowera mkati ya mikono 10 m’lifupi mwake.+ Panalinso kanjira ka mkono umodzi, kotuluka m’zipindazo kulowa m’njira ina ija. Makomo a zipindazo analoza mbali ya kumpoto. 5 Zipinda zodyeramo zam’mwamba zinali zocheperapo chifukwa chakuti makondewo anatengako malo ena a zipindazo. Zipinda zimenezi zinali zocheperapo kusiyana ndi zapakati komanso zapansi. 6 Zipindazo zinali m’mizere itatu yosanjikizana+ ndipo zinalibe zipilala ngati za m’mabwalo. N’chifukwa chake zipinda zam’mwamba zinali zazing’ono kusiyana ndi zipinda zapakati komanso zapansi.

7 Mpanda wamiyala umene unali kunja, unali pafupi ndi zipinda zodyeramo zimene zinali mbali ya kubwalo lakunja, moyang’anizana ndi zipinda zina zodyeramo. Mpandawo unali mikono 50 m’litali mwake. 8 Zipinda zodyeramo zimene zinali kumbali ya bwalo lakunja zinali mikono 50 m’litali mwake, ndipo zimene zinali mbali ya ku kachisi zinali mikono 100 m’litali mwake. 9 Kum’mawa kwa zipinda zapansi za nyumba yodyeramo, kunali khomo limene munthu anali kulowera kuchokera m’bwalo lakunja.

10 Kumbuyo kwa mpanda wamiyala wa bwalo umene unali mbali ya kum’mawa, moyang’anizana ndi mpata waukulu+ komanso nyumba imene inali kumadzulo, kunali zipinda zodyeramo.+ 11 Kutsogolo kwa zipinda zodyeramozo kunali njira yofanana ndi ya zipinda zodyeramo za mbali ya kumpoto. M’litali ndi m’lifupi mwa zipindazo munali mofanana ndi mwa zipinda za kumpoto.+ Makomo otulukira a zipindazo, kamangidwe ka zipindazo ndiponso makomo ake olowera, zinali zofanana ndi zipinda za kumpoto zija. 12 Khomo limene linali koyambirira kwa njira, linali lofanana ndi makomo a zipinda zodyeramo zimene zinali mbali ya kum’mwera. Munthu akamabwera kuzipindazo anali kudutsa m’njira imeneyi, yomwe inali m’mphepete mwa mpanda wamiyala umene unali kum’mawa.+

13 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Zipinda zodyeramo za kumpoto ndi za kum’mwera zimene zili moyang’anizana ndi mpata waukulu+ ndi zopatulika. M’zipinda zimenezi, ansembe otumikira+ Yehova amadyeramo zinthu zopatulika koposa.+ Mmenemo amaikamo zinthu zopatulika koposa, nsembe yambewu, nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula, chifukwa malo amenewa ndi oyera.+ 14 Ansembe akalowa m’zipindazo asamatuluke m’malo oyerawo kupita kubwalo lakunja. Akafuna kutuluka, zovala zawo zimene amavala nthawi zonse potumikira,+ azizisiya m’zipindazo chifukwa n’zopatulika. Ndiyeno azivala zovala zina+ n’kupita kumene kuli anthu.”

15 Choncho anamaliza kuyeza nyumba yamkati, ndipo ananditulutsa kudzera pachipata chimene chinayang’ana kum’mawa.+ Kenako anayeza malo onsewo.

16 Iye anayeza mbali ya kum’mawa ndi bango loyezera+ ndipo malo onsewo anakwana mabango 500.

17 Anayezanso mbali ya kumpoto ndi bango loyezera ndipo malo onsewo anakwana mabango 500.

18 Anayezanso mbali ya kum’mwera ndi bango loyezera ndipo malowo anakwana mabango 500.

19 Kenako anazungulira kupita mbali ya kumadzulo. Kumeneko anayeza malowo ndi bango loyezera ndipo anakwana mabango 500.

20 Anayeza malo onsewo mbali zonse zinayi. Malo onsewo anali ndi mpanda+ wokwana mabango 500 m’litali ndi mabango 500 m’lifupi mwake.+ Mpandawo unali kusiyanitsa zinthu zopatulika ndi zinthu zodetsedwa.+

43 Kenako munthu uja ananditengera kuchipata chimene chinayang’ana kum’mawa.+ 2 Kumeneko ndinaona ulemerero+ wa Mulungu wa Isiraeli ukubwera kuchokera kumbali ya kum’mawa.+ Mawu ake anali kumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri,+ ndipo dziko lapansi linawala chifukwa cha ulemerero wake.+ 3 Zimene ndinaonazo zinali zofanana ndi zimene ndinaona m’masomphenya ena.+ Zinali zofanana ndi masomphenya amene ndinaona pamene ndinapita kukawononga mzinda.*+ Ndinaona zinthu zofanana ndi zimene ndinaona m’mphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.

4 Ndiyeno ulemerero+ wa Yehova unalowa m’Nyumbayo kudzera pachipata choyang’ana kum’mawa.+ 5 Kenako mzimu unandidzutsa+ m’kupita nane kubwalo lamkati. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza m’Nyumba ija.+ 6 Tsopano ndinayamba kumva wina akulankhula nane kuchokera m’Nyumbamo.+ Apa n’kuti munthu uja ataima pambali panga.+ 7 Pamenepo Mulungu anandiuza kuti:

“Iwe mwana wa munthu, malo awa ndi malo a mpando wanga wachifumu+ ndiponso poikapo mapazi anga.+ Ndidzakhala pamalo amenewa, pakati pa ana a Isiraeli mpaka kalekale.+ A nyumba ya Isiraeli ndi mafumu awo+ sadzaipitsanso dzina langa loyera+ ndi dama lawo komanso ndi mitembo+ ya mafumu awo.* 8 Sadzaipitsanso dzina langa poika khomo lawo pafupi ndi khomo langa. Sadzaikanso felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine n’kungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.+ Iwo anaipitsa dzina langa loyera ndi zinthu zawo zonyansa zimene anali kuchita+ moti ndinawafafaniza nditakwiya.+ 9 Tsopano aleke dama+ lawo ndi kuchotsa mitembo ya mafumu awo n’kukaiika kutali ndi ine.+ Akatero ine ndidzakhala pakati pawo mpaka kalekale.+

10 “Koma iwe mwana wa munthu, uza nyumba ya Isiraeli za Nyumba+ ino kuti achite manyazi chifukwa cha zolakwa zawo,+ ndipo adzayeze nyumbayi ndi kudziwa tsatanetsatane wa kamangidwe kake. 11 Iwo akachita manyazi chifukwa cha zonse zimene anachita, ujambule chithunzi cha kamangidwe ka Nyumbayi+ iwo akuona. Usonyeze maonekedwe ake, makomo ake olowera ndi otulukira, zithunzi za kamangidwe kake ndi miyezo yake yonse. Uwadziwitse malamulo ake onse kuti aone kamangidwe ka nyumbayi ndi miyezo yake yonse kuti azizitsatira.+ 12 Lamulo lokhudza Nyumbayi ndi ili: Malo onse a pamwamba pa phiri kuzungulira nyumbayi ndi oyera koposa.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza Nyumbayi.

13 “Nayi miyezo ya guwa lansembe loyezedwa pogwiritsa ntchito muyezo wa mkono+ ndi chikhato.+ Miyezo ya chigawo chapansi cha guwa lansembe inali motere: Kuchokera pansi kufika pamwamba, chinali mkono umodzi. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa cha pamwamba pake. M’mphepete mwa chigawo chimenechi munali kakhoma kakatali chikhatho* chimodzi. 14 Chigawo chachiwiri chimene chinali pamwamba pa chigawo choyambacho chinali chachitali mikono iwiri. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa chimene chinali pamwamba pake. Chigawo chachitatu chinali chachitali mikono inayi. Chigawo chimenechi chinali chokulirapo m’mbali ndi mkono umodzi kuposa chimene chinali pamwamba pake. 15 Malo osonkhapo moto anali pachigawo cha pamwamba penipeni pa guwalo. Chigawo chimenechi chinali chachitali mikono inayi. M’mbali mwa malo osonkhapo motowo munali nyanga zinayi.+ 16 Chigawo cha malo osonkhapo motocho chinali chofanana mbali zonse zinayi.+ M’litali mwake chinali mikono 12 ndipo m’lifupi mwake chinalinso mikono 12.+ 17 Chigawo chachitatu chinali mikono 14 m’litali ndiponso mikono 14 m’lifupi mbali zonse zinayi. Kakhoma ka m’mphepete mwake kanali kakatali hafu ya mkono, ndipo pansi pake kanali mkono umodzi kuzungulira chigawo chonsecho.

“Guwalo linali ndi masitepe oyang’ana mbali ya kum’mawa.”

18 Munthu uja anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Amenewa ndi malamulo a guwa lansembe amene anaperekedwa pa nthawi imene analipanga. Guwali analipanga kuti aziperekerapo nsembe zopsereza zathunthu+ ndi kuwazapo magazi.’+

19 “‘Ansembe achilevi+ omwe ndi ana a Zadoki,+ amene amayandikira kwa ine ndi kunditumikira,+ uwapatse ng’ombe yaing’ono yamphongo kuchokera pagulu la ziweto kuti ikhale nsembe yamachimo.’+ Watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 20 ‘Utengeko magazi akewo n’kuwapaka panyanga zinayi za guwa lansembe ndi m’makona anayi a chigawo chachitatu cha guwalo. Magaziwo uwapakenso pakakhoma konse kozungulira chigawo chachitatucho. Uchite zimenezi kuti uyeretse guwa lansembelo ku machimo+ ndipo uliperekere nsembe yophimba machimo.+ 21 Kenako utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo ya nsembe yamachimo. Ndiyeno wina akapsereze ng’ombeyo pamalo opserezera a pa Nyumbayo, kunja kwa malo opatulika.+ 22 Pa tsiku lachiwiri, udzabweretse mbuzi yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yamachimo. Ansembewo adzayeretse guwa lansembelo ku machimo monga mmene analiyeretsera ku machimo popereka ng’ombe yaing’ono yamphongo.’

23 “‘Pomaliza mwambo woyeretsa guwalo ku machimo, udzatenge ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema pagulu la ziweto n’kuzibweretsa kuno. 24 Udzazibweretse pamaso pa Yehova ndipo ansembe adzaziwaze mchere n’kuzipereka+ kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. 25 Kwa masiku 7 uzipereka mbuzi yamphongo monga nsembe yamachimo tsiku lililonse.+ Ansembe azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo ndi nkhosa yamphongo. Nyama zimenezi zizichokera pagulu la ziweto ndipo zizikhala zopanda chilema. 26 Kwa masiku 7, aphimbe machimo+ a guwalo ndipo aliyeretse ndi kuyamba kuligwiritsa ntchito. 27 Masiku 7 amenewo akatha, kuyambira pa tsiku la 8+ kupita m’tsogolo, ansembe azidzakuperekerani nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zachiyanjano paguwali, ndipo ine ndidzasangalala nanu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

44 Kenako munthu uja ananditengeranso kuchipata chakunja cha malo opatulika, chimene chinayang’ana kum’mawa,+ ndipo tinapeza kuti chinali chotseka.+ 2 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Chipata ichi chizikhalabe chotseka. Sichidzatsegulidwa, ndipo munthu wamba sadzalowa kudzera pachipata chimenechi chifukwa chakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli,+ walowa kudzera pachipata chimenechi. Choncho chidzapitirizabe kukhala chotseka. 3 Koma mtsogoleri+ wa anthu azidzakhala m’chipata chimenechi kuti azidzadya chakudya pamaso pa Yehova.+ Azidzalowa mmenemo kudzera kukhonde la kanyumba ka pachipata ndipo azidzatulukiranso komweko.”+

4 Kenako ananditengera kutsogolo kwa Nyumba ija kudzera pachipata cha kumpoto kuti ndikaone zimene zinali kumeneko. Kumeneko ndinaona ulemerero wa Yehova utadzaza m’nyumba ya Yehova.+ Pamenepo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ 5 Tsopano Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, khala tcheru+ ndipo uone ndi maso ako. Umve ndi makutu ako zonse zimene ndikukuuza zokhudza malangizo ndi malamulo onse a nyumba ya Yehova. Uonetsetse khomo la Nyumbayi ndi zipata zonse zotulukira m’malo opatulikawa. 6 Uuze anthu opandukawo,+ inde uuze a nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mwanyanya kuchita zinthu zonyansa, inu a nyumba ya Isiraeli.+ 7 Mumatenga alendo osachita mdulidwe wa mtima ndi mdulidwe wa khungu lawo+ kuti alowe m’malo anga opatulika ndi kuwadetsa. Ndithu iwo amadetsa nyumba yanga. Pamene mukupereka chakudya+ changa chomwe ndi mafuta+ ndi magazi,+ pangano langa limaphwanyidwa chifukwa cha zonyansa zanu zonse.+ 8 Inu simunakwaniritse utumiki wanu wosamalira zinthu zanga zopatulika,+ ndipo simunasankhe ena kuti azinditumikira pamalo anga opatulika m’malo mwa inu.”’+

9 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mlendo aliyense amene ali pakati pa ana a Isiraeli, wosachita mdulidwe wa mtima ndi mdulidwe wa khungu, asalowe m’malo anga opatulika.”’+

10 “‘Koma Alevi amene anachoka kwa ine n’kupita kutali+ adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo. Iwo anachoka kwa ine pamene Aisiraeli anandisiya n’kutsatira mafano awo onyansa.+ 11 Kenako Aleviwo adzakhala atumiki m’malo anga opatulika. Adzakhala ndi maudindo oyang’anira zipata za Nyumba ino ndipo adzakhala atumiki a pa Nyumbayi.+ Iwo azidzapha nyama za nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zina za anthu+ ndipo adzaimirira pamaso pa anthuwo ndi kuwatumikira.+ 12 Ine ndatambasula dzanja langa kuti ndiwalange+ chifukwa chakuti anali kutumikira anthu pamaso pa mafano awo onyansa.+ Iwo anakhala chopunthwitsa kwa anthu a nyumba ya Isiraeli ndipo anawachititsa zinthu zoipa,+ choncho adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 13 ‘Sadzayandikira kwa ine kuti anditumikire monga ansembe kapena kuyandikira zinthu zanga zilizonse zopatulika, zomwe ndi zoyera koposa.+ Iwo adzanyozeka ndi kukumana ndi zotsatira za zonyansa zimene anachita.+ 14 Ine ndidzawaika kuti azidzachita utumiki wa pa Nyumbayi wokhudza ntchito zake zonse ndi zonse zoyenera kuchitika mmenemo.’+

15 “‘Ansembe achilevi,+ ana a Zadoki,+ amene anali kugwira ntchito za pamalo anga opatulika pamene ana a Isiraeli anachoka kwa ine n’kupita kutali,+ amenewa adzandiyandikira ndi kunditumikira. Iwo adzaima pamaso panga+ ndi kundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 ‘Iwo ndi amene adzalowe m’malo anga opatulika,+ ndipo adzayandikira tebulo* langa ndi kunditumikira.+ Amenewa adzachita utumiki wawo kwa ine.+

17 “‘Iwo akafuna kulowa m’tinyumba ta zipata za bwalo lamkati, azivala zovala zansalu. Asamavale zovala zaubweya wa nkhosa pamene akutumikira m’tinyumba ta zipata za bwalo lamkati komanso mkati mwenimwenimo.+ 18 Iwo azivala zovala za kumutu zansalu+ ndi makabudula ansalu.+ Asamavale zovala zochititsa thukuta. 19 Akafuna kupita kubwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zawo zimene anavala potumikira.+ Aziika zovalazo m’zipinda zopatulika zodyeramo+ ndipo azivala zovala zina kuti asayeretse anthu ndi zovala zawozo.+ 20 Asamamete tsitsi la kumutu kwawo,+ komanso tsitsilo lisamatalike kwambiri, chotero tsitsilo azilidulira.+ 21 Ansembe asamamwe vinyo ngati akukalowa m’bwalo lamkati.+ 22 Iwo asamatenge mkazi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati kuti akhale mkazi wawo,+ koma azitenga anamwali omwe ndi ana ochokera m’nyumba ya Isiraeli+ kapena azitenga mkazi wamasiye amene anali mkazi wa wansembe.’

23 “‘Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu choipitsidwa. Aziwaphunzitsa kuti adziwe kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi choyera.+ 24 Iwo aziimirira pa mlandu ndi kuweruza.+ Aziweruza motsatira zigamulo zanga.+ Azisunga malamulo ndi malangizo anga okhudza zikondwerero zanga zonse,+ ndipo aziyeretsa masabata anga.+ 25 Asamapite kumene kuli munthu wakufa kuti angakhale odetsedwa. Koma wansembe akhoza kudzidetsa chifukwa cha bambo ake, mayi ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, m’bale wake kapena mlongo wake amene sanakwatiwepo.+ 26 Akamaliza kudziyeretsa, azimuwerengera masiku 7.+ 27 Pa tsiku limene adzalowe m’malo oyera, m’bwalo lamkati, kuti adzatumikire m’malo oyerawo, adzapereke nsembe yake yamachimo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

28 “‘Ponena za cholowa chawo, ineyo ndiye cholowa chawo.+ Anthu inu musawapatse chilichonse kuti chikhale chuma chawo mu Isiraeli, chuma chawo ndine. 29 Iwowa ndi amene azidzadya nsembe yambewu, nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula.+ Chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mu Isiraeli chidzakhala chawo.+ 30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira za mtundu uliwonse ndi zopereka zanu zonse za mtundu uliwonse zabwino kwambiri zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wochokera ku mbewu zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe+ kuti madalitso abwere panyumba yanu.+ 31 Ansembe asamadye nyama iliyonse imene aipeza yakufa, asamadye chouluka chilichonse kapena nyama iliyonse imene yakhadzulidwa ndi chilombo.’+

45 “‘Anthu inu, pogawana dzikoli kuti likhale cholowa chanu,+ mudzapatule malo ena ndi kuwapereka kwa Yehova+ monga gawo loyera.+ M’litali mwa malo amenewo mudzakhale mikono 25,000, ndipo m’lifupi mudzakhale mikono 10,000.+ Malo onsewo adzakhale gawo loyera. 2 Pamalo amenewa padzakhale malo oyera okwana mikono 500 m’litali ndi mikono 500 m’lifupi. Malowa adzakhale ofanana mbali zonse.+ Kumbali zake zonse kudzakhale malo odyetserako ziweto okwana mikono 50.+ 3 Kuchokera pa miyezo ya malo amenewa, udzayeze malo okwana mikono 25,000 m’litali ndi mikono 10,000 m’lifupi. M’malo amenewa mudzakhale malo opatulika amene ndi malo oyera koposa.+ 4 Malo oyerawa adzakhale gawo la ansembe m’dzikoli.+ Ansembewo ndi atumiki a pamalo opatulika ndipo amayandikira kwa Yehova ndi kumutumikira.+ Malo amenewa adzakhale awo kuti adzamangepo nyumba zawo. Adzakhalenso malo opatulika omangapo nyumba yopatulika.

5 “‘Kudzakhalenso malo okwana mikono 25,000 m’litali ndi mikono 10,000 m’lifupi.+ Malo amenewa adzakhale a Alevi, atumiki a pa Nyumbayo. Aleviwo adzakhale ndi zipinda 20 zodyeramo chakudya.+

6 “‘Anthu inu mudzapereke malo okwana mikono 5,000 m’lifupi ndi mikono 25,000 m’litali kuti adzakhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhale moyandikana ndi chopereka chopatulika,+ ndipo adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.

7 “‘Malo a mtsogoleri wa anthu adzakhale kumbali iyi ndi kumbali ina ya chopereka chopatulika+ ndi ya malo a mzinda. Adzakhale pafupi ndi chopereka chopatulika komanso pafupi ndi malo a mzindawo. Malo a mtsogoleriwo adzakhale kumadzulo ndi kum’mawa. M’litali mwake adzakhale ofanana ndi magawo a malo amene mafuko a Isiraeli adzalandire, kuchokera kumalire a kumadzulo kukafika kumalire a kum’mawa.+ 8 Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli. Atsogoleri anga sadzazunzanso anthu anga,+ ndipo adzagawa dzikoli kwa anthu a nyumba ya Isiraeli malinga ndi mafuko awo.’+

9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!’+

“‘Siyani ziwawa ndi kulanda zinthu za anthu anga.+ Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10 ‘Anthu inu muzikhala ndi masikelo olondola, muyezo wa efa* wolondola ndi mitsuko* yoyezera yolondola.+ 11 Muyezo wa efa ndi wa mtsuko woyezera uzikhala wofanana komanso wosasinthasintha. Muyezo wa mtsuko uzikhala wokwanira gawo limodzi mwa magawo 10 a homeri.* Gawo limodzi mwa magawo 10 la muyezo wa homeri lizifanana ndi muyezo wa efa.+ Muzipeza miyezo yoyenera ya zimenezi potengera muyezo wa nthawi zonse wa homeri. 12 Sekeli+ limodzi lizikwana magera 20.+ Muzitenga masekeli 20, masekeli 25 ndi masekeli 15 kuti ukhale muyezo wanu wa mane.’

13 “‘Pa tirigu wanu wokwana homeri, muzitengapo gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa kuti likhale chopereka chanu. Pa balere wanu wokwana homeri muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. 14 Poyeza mafuta oti muzipereka, muzigwiritsa ntchito mtsuko woyezera monga muyezo wanu wa nthawi zonse. Mtsukowo uzikwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa kori.* Mitsuko 10 izikwana homeri chifukwa mitsuko 10 imakwana homeri. 15 Muzipereka nkhosa imodzi kuchokera pagulu la nkhosa zanu. Muzipereka nkhosa imodzi pa ziweto 200 zilizonse mu Isiraeli.+ Muzipereka nsembe zimenezi pamodzi ndi nsembe zambewu,+ nsembe yopsereza yathunthu+ ndi nsembe zachiyanjano+ kuti muziphimba machimo a anthu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

16 “‘Anthu onse a m’dzikoli azidzapereka zopereka zimenezi+ kwa mtsogoleri mu Isiraeli.+ 17 Mtsogoleri+ wa anthu adzapatsidwa udindo woyang’anira nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa.+ Iye azidzayang’anira nsembezo pa nthawi ya zikondwerero,+ pa masiku okhala mwezi,+ pa nthawi ya masabata+ ndi pa nthawi ya zikondwerero zonse za nyumba ya Isiraeli.+ Mtsogoleriyo ndi amene azidzapereka kwa ansembe nyama za nsembe yamachimo, nsembe yambewu, nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zachiyanjano kuti aphimbe machimo a nyumba ya Isiraeli.’

18 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘M’mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, uzitenga ng’ombe yamphongo yaing’ono yopanda chilema+ kuchokera pagulu la ziweto, ndipo uziyeretsa malo opatulika ku machimo.+ 19 Wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimo ndi kuwapaka pafelemu+ la Nyumbayi ndi pamakona anayi a chigawo chachitatu cha guwa lansembe.+ Aziwapakanso pafelemu la kanyumba ka pachipata cha bwalo lamkati. 20 Muzichitanso zimenezi pa tsiku la 7 la mweziwo chifukwa cha munthu aliyense amene walakwa komanso chifukwa cha munthu aliyense amene walakwitsa+ zinthu chifukwa chosadziwa. Anthu inu muziperekera Nyumbayi nsembe yophimba machimo.+

21 “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo, muzichita pasika.+ Muzichita chikondwerero chimenechi kwa masiku 7 ndipo muzidya mikate yopanda chofufumitsa.+ 22 Pa tsiku limeneli, mtsogoleri azipereka kwa ansembe ng’ombe yaing’ono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo ake ndi a anthu onse a m’dzikoli.+ 23 Kwa masiku 7 a chikondwererocho,+ iye azipatsa ansembe nyama zoti ziperekedwe kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. Azipereka ng’ombe zazing’ono zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7. Nyama zimenezi zizikhala zopanda chilema ndipo azizipereka tsiku ndi tsiku kwa masiku 7.+ Aziperekanso mbuzi yamphongo tsiku ndi tsiku monga nsembe yamachimo.+ 24 Popereka ng’ombe iliyonse yaing’ono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka nkhosa iliyonse yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Pa muyezo uliwonse wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+

25 “‘M’mwezi wa 7, pa tsiku la 15 la mweziwo, pa nthawi ya chikondwerero,+ mtsogoleri azipereka kwa wansembe zinthu zofanana ndi zimenezi kwa masiku 7.+ Azipereka nsembe yamachimo yofanana ndi imeneyi, nsembe zopsereza zathunthu zofanana ndi zimenezi, nsembe yambewu yofanana ndi imeneyi ndiponso mafuta ofanana ndi amenewa.’”

46 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chipata choyang’ana kum’mawa cha bwalo lamkati+ chizikhala chotseka+ kwa masiku ogwira ntchito 6.+ Pa tsiku la sabata, ndi pa tsiku lokhala mwezi chipatacho chizitsegulidwa.+ 2 Mtsogoleri wa anthu azilowa kuchokera panja n’kufika pakhonde la kanyumba ka pachipata+ ndipo aziima pafupi ndi felemu la chipatacho.+ Ndiyeno ansembe azimuperekera nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zachiyanjano. Mtsogoleriyo azigwada ndi kuwerama pakhomo la kanyumba ka pachipata,+ kenako azituluka koma chipatacho chisamatsekedwe kufikira madzulo. 3 Anthu a m’dzikoli azigwada ndi kuwerama pamaso pa Yehova pakhomo la kanyumba ka pachipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa masiku okhala mwezi.+

4 “‘Nsembe yopsereza yathunthu imene mtsogoleri wa anthu azipereka kwa Yehova pa tsiku la sabata, izikhala ana a nkhosa amphongo okwana 6 ndi nkhosa yamphongo imodzi. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+ 5 Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa.+ Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse.+ Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+ 6 Pa tsiku lokhala mwezi,+ azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. Aziperekanso ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa imodzi yamphongo. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+ 7 Popereka ng’ombe yaing’ono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa, azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+

8 “‘Mtsogoleri+ wa anthu akamalowa, azidzera mbali ya kukhonde ya kanyumba ka pachipata. Potuluka azidzeranso komweko.+ 9 Anthu a m’dzikoli akafika pamaso pa Yehova kuti adzam’gwadire ndi kumuweramira pa nyengo za chikondwerero,+ munthu amene walowa kudzera pachipata cha kumpoto+ azidzatulukira pachipata cha kum’mwera.+ Amene walowera pachipata cha kum’mwera azidzatulukira pachipata cha kumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pachipata chimene analowera. Aliyense azidzangoyenda kupita kutsogolo mpaka kukatuluka. 10 Pamene anthuwo akulowa, mtsogoleri amene ali pakati pawo azilowa nawo limodzi, ndipo pamene akutuluka nayenso azituluka.+ 11 Pa nthawi ya zikondwerero+ ndi pa nyengo ya zikondwerero zanu, azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Aziperekanso nkhosa yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+

12 “‘Mtsogoleri wa anthu akapereka kwa ansembe nsembe yopsereza yathunthu+ kuti ikhale nsembe yaufulu, kapena akapereka nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova, munthu wina azimutsegulira chipata cha kum’mawa.+ Mtsogoleriyo azipereka kwa ansembe nsembe yake yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zachiyanjano mofanana ndi mmene amachitira pa tsiku la sabata.+ Akatero azituluka ndipo munthu wina azitseka chipatacho iye akatuluka.+

13 “‘Tsiku ndi tsiku uzipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo wopanda chilema wosakwanitsa chaka. Uzim’pereka m’mawa uliwonse monga nsembe yopsereza yathunthu yoperekedwa kwa Yehova.+ 14 Popereka kwa ansembe mwana wa nkhosayo, uziperekanso nsembe yambewu m’mawa uliwonse yokwanira gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Uziperekanso mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini kuti aziwawaza mu ufa wosalala.+ Lamulo lopereka nsembe yambewu kwa Yehova nthawi zonse lidzakhalapo mpaka kalekale. 15 M’mawa uliwonse, iwo azipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo, nsembe yambewu ndi mafuta, kuti zikhale nsembe yopsereza yathunthu ya nthawi zonse.’

16 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Mtsogoleri wa anthu akapereka mphatso kwa mwana wake aliyense wamwamuna monga cholowa chake, mphatsoyo idzakhala chuma cha mwanayo. Chimenecho ndi chuma cha anawo ndipo chidzakhala cholowa chawo. 17 Koma akapereka cholowa kwa mmodzi wa antchito ake ngati mphatso kuchokera pa cholowa chake, cholowacho chidzakhala cha wantchitoyo mpaka chaka cha ufulu,+ kenako chidzabwezedwa kwa mtsogoleriyo. Koma cholowa choperekedwa kwa ana ake chidzakhala chawo mpaka kalekale. 18 Mtsogoleri wa anthu asamatenge cholowa chilichonse cha anthu ndi kuwakakamiza kuchoka m’malo awo.+ Ana ake aamuna aziwapatsa cholowa kuchokera pamalo amene ali nawo, kuti anthu anga asamwazikane ndi kuchoka m’malo awo.’”+

19 Kenako munthu uja ananditenga n’kundilowetsa pakhomo+ limene linali pafupi ndi chipata chopita kuzipinda zodyeramo zopatulika. Zipindazi zinali za ansembe ndipo zinayang’ana kumpoto.+ M’mbali mwa zipindazo, kumbali ya kumadzulo ndinaonako malo. 20 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Amenewa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe ya kupalamula+ ndi nsembe yamachimo,+ komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja ndi kuyeretsa anthu.”+

21 Kenako ananditengera kubwalo lakunja ndi kundipititsa pansanamira zinayi za m’makona a bwalolo. Kumeneko ndinaona kuti pafupi ndi nsanamira yoyamba ya pakona panali bwalo, chimodzimodzinso pafupi ndi nsanamira inayo. 22 M’makona onse anayi a bwalolo munali mabwalo ang’onoang’ono okwana mikono 40 m’litali ndi mikono 30 m’lifupi. Mabwalo onsewo anali ndi miyezo yofanana, ndipo anali ndi tinyumba tapakona. 23 Panali kakhoma kamiyala kuzungulira mkati monse mwa tinyumba tonse tinayi tapakonato. M’munsi monse mwa kakhoma kameneko munali malo ophikirapo.+ 24 Kenako anandiuza kuti: “Izi ndi nyumba zowiritsiramo nyama. Kumeneku n’kumene atumiki a pa Nyumbayi amawiritsirako nsembe zimene anthu amapereka.”+

47 Kenako ananditenga n’kupita nanenso kukhomo la Nyumbayo.+ Kumeneko ndinaona madzi+ akutuluka pansi, pakhomo penipeni pa Nyumbayo chakum’mawa,+ pakuti Nyumbayo inayang’ana kum’mawa. Madziwo anali kutuluka pansi n’kumatsetsereka. Anali kutuluka kuchokera kumbali ya kudzanja lamanja kwa Nyumbayo, n’kudutsa kum’mwera kwa guwa lansembe.

2 Pambuyo pake ananditenga n’kutuluka nane kudzera pachipata chakumpoto.+ Kumeneko tinadutsa njira yakunja n’kuzungulira kukafika kuchipata chakunja chimene chinayang’ana kum’mawa.+ Kuchipata chimenecho tinaona madzi+ akuyenda kuchokera kumbali ya kudzanja lamanja kwa chipatacho.

3 Ndiyeno munthu uja anapita mbali ya kum’mawa atatenga chingwe choyezera m’manja mwake.+ Kenako anayeza mtsinjewo mikono 1,000 kuchokera pa Nyumba ija, ndipo anandiuza kuti ndiwoloke mtsinjewo. Madziwo anali olekeza m’mapazi.

4 Kuchokera pamenepo anayeza mtsinjewo mikono 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madziwo anafika m’mawondo.

Anayezanso mtsinjewo mikono 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madziwo anafika m’chiuno.

5 Kuchokera pamenepo anayezanso mtsinjewo mikono 1,000. Mtsinjewo unakula kwambiri moti sindinathe kuwoloka. Izi zinali choncho chifukwa chakuti madzi ake anazama kwambiri ndipo anali ofunika kusambira. Chotero unakhala mtsinje waukulu woti munthu sangathe kuwoloka.

6 Pamenepo anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi?”

Kenako munthu uja ananditulutsa m’madzimo n’kupita nane m’mphepete mwa mtsinjewo. 7 Nditatuluka m’madzimo ndinangoona kuti m’mphepete mwa mtsinjewo munali mitengo yambirimbiri kumbali iyi ndi kumbali inayo.+ 8 Ndiyeno anandiuza kuti: “Madzi awa akupita kuchigawo cha kum’mawa, ndipo adutsa ku Araba+ n’kukafika kunyanja.+ Madziwa akakafika kunyanjako,+ akachititsa madzi a m’nyanjamo kukhala abwino. 9 Zikatero zamoyo zam’madzi za mtundu uliwonse zidzatha kukhala m’madzimo,+ kulikonse kumene mtsinje waukuluwu ukupita. Nsomba zidzachuluka chifukwa madzi amenewa adzafika kunyanjako. Madzi a m’nyanjayo adzakhala abwino+ ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, zinthu zidzakhala zamoyo.

10 “Asodzi adzaimirira m’mbali mwa nyanjayo kuchokera ku Eni-gedi+ mpaka ku Eni-egilaimu. Kumeneko kudzakhala malo oyanikapo makoka. Nsombazo zidzakhala zambirimbiri, zamitundu yosiyanasiyana ngati nsomba za ku Nyanja Yaikulu.+

11 “Koma madzi a m’matawale ndi m’madambo a m’mphepete mwa nyanjayo sadzasintha n’kukhala abwino.+ Madzi amenewo adzakhalabe amchere.+

12 “M’mbali mwa mtsinjewo mudzamera mitengo yosiyanasiyana ya zipatso. Mitengoyo idzamera m’mphepete mwenimweni kumbali iyi ndi mbali inayo.+ Masamba ake sadzafota+ ndipo zipatso zake sizidzatha.+ Mitengo imeneyo izidzabereka zipatso mwezi ndi mwezi chifukwa chakuti madzi ake akuchokera m’malo opatulika.+ Zipatso zake zidzakhala chakudya ndipo masamba ake adzakhala mankhwala.”+

13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inuyo mutenge dera limeneli kuti likhale cholowa chanu. Limeneli likhale dziko la mafuko 12 a Isiraeli. Zigawo ziwiri zikhale za mbadwa za Yosefe.+ 14 Anthu inu muyenera kutenga dziko limeneli monga cholowa chanu. Inetu ndinalumbira nditakweza dzanja+ kuti ndidzapereka dziko limeneli kwa makolo anu.+ Choncho mugawane dzikoli mwa kuchita maere kuti likhale cholowa chanu. Aliyense alandire gawo lofanana ndi la m’bale wake.+

15 “Malire a dzikoli, kumbali ya kumpoto, ayambire ku Nyanja Yaikulu kudzera njira ya ku Heteloni+ mpaka kukafika ku Zedadi,+ 16 ku Hamati,+ ku Berota,+ ku Siburaimu kumene ndi kumalire a Damasiko+ ndi Hamati. Malirewo akafikenso ku Hazere-hatikoni kufupi ndi malire a Haurani.+ 17 Malire ochokera kunyanja akafike ku Hazara-enoni,+ kumene ndi kumalire a Damasiko, mpaka kukafika kumpoto kwake, komanso kumalire a Hamati.+ Amenewa akhale malire a mbali ya kumpoto.

18 “Malire a mbali ya kum’mawa ayambire pakati pa Haurani+ ndi Damasiko+ n’kutsetsereka ndi mtsinje wa Yorodano+ pakati pa Giliyadi+ ndi dziko la Isiraeli. Anthu inu muyeze mtunda kuchokera kumalirewo kukafika kunyanja ya kum’mawa. Amenewa akhale malire a mbali ya kum’mawa.

19 “Malire a mbali ya kum’mwera, ayambire ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa*+ cha Iguputo mpaka ku Nyanja Yaikulu. Amenewa akhale malire a mbali ya kum’mwera, cha ku Negebu.

20 “Kumbali ya kumadzulo malire anu akhale Nyanja Yaikulu, kuyambira m’malire a mbali ya kum’mwera mpaka kukafika kumalire a Hamati.+ Amenewa akhale malire a mbali ya kumadzulo.”

21 “Inu mugawane dzikoli pakati pa mafuko onse 12 a Isiraeli. 22 Mugawane dzikoli kuti likhale cholowa chanu+ ndi cha alendo okhala pakati panu, amene abereka ana pakati panu.+ Alendowo akhale ngati nzika pakati pa ana a Isiraeli. Iwo apatsidwe cholowa pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Isiraeli.+ 23 Mlendo aliyense mum’patse cholowa m’fuko limene akukhala monga mlendo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

48 “Mayina a mafuko ndi awa. Fuko la Dani+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kumalire a kumpoto a dzikolo, m’mbali mwa msewu wa ku Heteloni+ wopita kumalire a Hamati.+ Malire a gawolo chakumpoto, akafikenso ku Hazara-enani,+ kumalire a Damasiko kufupi ndi Hamati. Gawolo likhale ndi malire kumbali ya kum’mawa ndi kumbali ya kumadzulo. 2 Fuko la Aseri+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Dani. 3 Fuko la Nafitali+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Aseri. 4 Fuko la Manase+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Nafitali. 5 Fuko la Efuraimu+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Manase. 6 Fuko la Rubeni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Efuraimu. 7 Fuko la Yuda+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Rubeni. 8 Anthu inu mupereke gawo lina monga chopereka chanu. Gawolo lichite malire ndi gawo la fuko la Yuda ndipo likhale mikono 25,000 m’lifupi.+ M’litali mwake lifanane ndi magawo a mafuko aja. Malire a gawolo ayambire kum’mawa kukafika kumadzulo. Malo opatulika akhale pakati pa gawo limeneli.+

9 “Gawo loti mupereke kwa Yehova monga chopereka chanu likhale mikono 25,000 m’litali, ndipo m’lifupi likhale mikono 10,000. 10 Gawo limeneli likhale chopereka chopatulika cha ansembe.+ Mbali ya kumpoto, gawoli likhale mikono 25,000 m’litali mwake. Mbali ya kumadzulo likhale mikono 10,000 m’lifupi. Mbali ya kum’mawa likhale mikono 10,000 m’lifupi, ndipo mbali ya kum’mwera gawoli likhale mikono 25,000 m’litali. Pakati pa gawo limeneli pakhale malo opatulika a Yehova.+ 11 Gawo limeneli likhale la ansembe opatulika, ana a Zadoki,+ amene amanditumikira. Iwo sanandisiye ngati mmene anandisiyira Alevi amene anatsata ana a Isiraeli.+ 12 Ansembewo akhale ndi gawo lawo kuchokera pa gawo limene mupereke. Gawolo likhale lopatulika koposa ndipo lichite malire ndi gawo la Alevi.+

13 “Alevi akhale ndi gawo+ pafupi ndi gawo la ansembe. M’litali mwake likhale mikono 25,000 ndipo m’lifupi likhale mikono 10,000. Malo onsewo akhale aatali mikono 25,000 ndipo m’lifupi mwake akhale okwana mikono 10,000.+ 14 Aleviwo asagulitse mbali iliyonse ya malowo kapena kuwasinthanitsa ndi chilichonse. Aliyense asapereke malo abwino kwambiriwo kwa munthu wa fuko lina pakuti ndi malo opatulika kwa Yehova.+

15 “Malo otsala okwana mikono 5,000 m’lifupi ndi mikono 25,000 m’litali, akhale malo odetsedwa a mzinda.+ Malo amenewa akhale okhalamo anthu ndi odyetserako ziweto. Pakati pa malowa pakhale mzinda.+ 16 Miyezo ya mzindawo ikhale motere: Mbali ya kumpoto, mzindawo ukhale wautali mikono 4,500. Mbali ya kum’mwera ukhale wautali mikono 4,500. Mbali ya kum’mawa ukhale wautali mikono 4,500, ndipo mbali ya kumadzulo ukhalenso mikono 4,500. 17 Mzindawo ukhale ndi malo odyetserako ziweto.+ Mbali ya kumpoto malowo akhale aatali mikono 250. Mbali ya kum’mwera akhale mikono 250. Mbali ya kum’mawa akhale mikono 250, ndipo mbali ya kumadzulo malowo akhalenso mikono 250.

18 “Malo otsala akhale aatali mofanana ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika.+ Akhale mikono 10,000 kum’mawa ndiponso mikono 10,000 kumadzulo. Malo amenewo achite malire ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika. Zokolola za pamalowo zizikhala chakudya cha otumikira mumzindawo.+ 19 Anthu a mafuko onse a Isiraeli otumikira mumzinda ndiwo azidzalima malo amenewa.+

20 “Malo onse oti aperekedwewo akhale aatali mikono 25,000 mbali iyi ndi mikono 25,000 mbali inayo. Anthu inu mupereke malo ofanana mbali zonse kuti akhale chopereka chopatulika ndiponso malo a mzinda.

21 “Malo otsala a mbali iyi ndi mbali inayo ya chopereka chopatulika ndiponso ya mzinda+ akhale a mtsogoleri+ wa anthu. Kumbali ya kum’mawa, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Kumbali ya kumadzulo, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Malo a mtsogoleriwo achokere kumbali ya kum’mawa kukafika kumbali ya kumadzulo mofanana ndi magawo a mafuko aja.+ Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a Nyumba ija akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa.

22 “Malo a Alevi komanso malo a mzinda akhale pakati pa malo a mtsogoleri. Malo a mtsogoleriwo achite malire ndi gawo la fuko la Yuda+ komanso gawo la fuko la Benjamini.

23 “Pa mafuko ena otsalawo, fuko la Benjamini+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo. 24 Fuko la Simiyoni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Benjamini. 25 Fuko la Isakara+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Simiyoni. 26 Fuko la Zebuloni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Isakara. 27 Fuko la Gadi+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Zebuloni. 28 Malire a kum’mwera a dzikolo akhale malire a gawo la fuko la Gadi a mbali ya kum’mwera. Malirewo achokere ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa+ cha Iguputo, mpaka ku Nyanja Yaikulu.+

29 “Anthu inu mugawe dziko limeneli pakati pa mafuko onse a Isiraeli kuti likhale cholowa chawo+ ndi magawo awo,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

30 “Makomo otulukira mumzinda akhale motere: Malire a mbali ya kumpoto a mzindawo akhale mikono 4,500.+

31 “Mayina a zipata za mzinda akhale ofanana ndi mayina a mafuko a Isiraeli. Mbali ya kumpoto kukhale zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Rubeni, chipata chimodzi chotchedwa Yuda, ndi chipata chimodzi chotchedwa Levi.

32 “Malire a mzindawo a mbali ya kum’mawa akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Yosefe, chipata chimodzi chotchedwa Benjamini, ndi chipata chimodzi chotchedwa Dani.

33 “Malire a mzindawo a mbali ya kum’mwera akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Simiyoni, chipata chimodzi chotchedwa Isakara, ndi chipata chimodzi chotchedwa Zebuloni.

34 “Malire a mzindawo a mbali ya kumadzulo akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Gadi, chipata chimodzi chotchedwa Aseri, ndi chipata chimodzi chotchedwa Nafitali.

35 “Kuzungulira mzindawo pakhale mtunda wokwana mikono 18,000. Kuyambira pa tsiku limenelo, dzina la mzindawo lidzakhala lakuti, Yehova Ali Kumeneko.”+

Mwina wilo limodzi linali kulowa pakati pa wilo linzake mopingasana nalo. Chotero mawilowo anali ndi mbali zinayi.

Ena amati “anthota.”

Ena amati “wonzuna.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu amene tawamasulira kuti “tirigu wamtundu wina” akutanthauza mtundu wa tirigu wosakoma kwenikweni umene unali kulimidwa ku Iguputo kale.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.

Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.

Ena amati “masaka.”

Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”

Zikuoneka kuti nthambi imeneyi anali kuigwiritsa ntchito polambira mafano.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa Eze 1:16.

Mawu ake enieni, “mutu.”

Kapena kuti “anthu okhudzidwa ndi ufulu wako wowombolanso cholowa chako.”

Katumbu ndi nyama yaubweya yam’madzi ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka m’nyanja zikuluzikulu.

Ena amati, “masikiyo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.

Mawu ake enieni m’Chiheberi ndi, “mtengo wa mpesa umene uli m’magazi anu.”

Mawu ake enieni, “anadutsitsa pamoto.”

Kapena kuti “nthaka yonse ya dziko lapansi.”

Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “chisoti chachifumu.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Kuwomba m’manja chinali chizindikiro chosonyeza kunyoza kapena kunyogodola.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “chiuno.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Onani Zakumapeto 5.

Kapena kuti, “Ndidzadzipereka kwambiri chifukwa cha dzina langa loyera.”

“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu, ndipo “chikhatho” chinali masentimita 7.4. Kuphatikiza zimenezi zimakwana pafupifupi masentimita 51.8 ndipo zimaimira muyezo wotchedwa “mkono wautali.” Choncho bango loyezera la mikono 6 linali lalitali mamita 3.11.

Kapena kuti “patsindwi.”

Zikuoneka kuti mawu akuti “kachisi” akutanthauza “Malo Oyera.”

Zikuoneka kuti anachita zimenezi mwa kulosera kuti mzindawo udzawonongedwa.

Mawu ake enieni, “mitembo ya mafumu awo pa imfa yawo.”

Umenewu ndi utali wofanana ndi utali wochokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kukafika pansonga ya chala chaching’ono, mutatambasula chikhatho. Utali umenewu ndi wokwana masentimita 22.2.

Kapena kuti “Guwa lansembe.”

“Muyezo wa efa” ndi wofanana ndi chitini chamalita 22.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena