Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 2 Samuel 1:1-24:25
  • 2 Samueli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Samueli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Samueli

Samueli Wachiwiri

kapena, malinga ndi Baibulo lachigiriki la Septuagint, MAFUMU WACHIWIRI

1 Sauli atamwalira, ndiponso Davide atabwera kuchokera kokakantha Aamaleki,+ Davideyo anakhala ku Zikilaga+ masiku awiri. 2 Ndiyeno pa tsiku lachitatu anaona munthu wina+ akubwera kuchokera kumsasa, kwa Sauli. Iye anali atang’amba zovala zake+ komanso atadzithira dothi kumutu.+ Atafika kwa Davide, nthawi yomweyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ kenako anagona pansi.

3 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Wachokera kuti?” Poyankha iye anati: “Ndathawa kumsasa wa Isiraeli.” 4 Kenako Davide anamufunsa kuti: “Zayenda bwanji kumeneko? Chonde, ndiuze.” Iye anayankha kuti: “Anthu athawa kunkhondo komanso anthu ambiri agwa ndipo afa,+ ngakhalenso Sauli+ ndi mwana wake Yonatani+ afa.” 5 Pamenepo Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Iweyo wadziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afadi?”+ 6 Mnyamatayo anayankha kuti: “Ndinapezeka kuti ndili paphiri la Giliboa,+ ndipo ndinaona Sauli atatsamira mkondo+ wake. Zili choncho, ndinaona asilikali oyenda m’magaleta ndi asilikali okwera pamahatchi* akumuyandikira.+ 7 Sauliyo atatembenuka n’kundiona, anandiitana, ndipo ine ndinayankha kuti, ‘Ine mbuyanga!’ 8 Kenako anandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe ndani?’ Ine ndinamuyankha kuti, ‘Ndine Mwamaleki.’+ 9 Ndiyeno anandiuza kuti, ‘Bwera kuno chonde, undiphe pakuti zinthu zandivuta,* koma ndidakali ndi moyo.’+ 10 Choncho ndinapita pamene iye anali ndi kumupha,+ chifukwa ndinadziwa kuti sakhalanso ndi moyo popeza anali atavulala kwambiri. Kenako ndinatenga chisoti chachifumu+ chimene anavala ndi khoza limene linali kudzanja lake kuti ndibwere nazo kuno kwa inu mbuyanga.”

11 Davide atamva zimenezi anagwira zovala zake ndi kuzing’amba.+ Nawonso amuna onse amene anali ndi Davide anang’amba zovala zawo. 12 Atatero, anayamba kulira ndi kubuma+ komanso kusala kudya+ mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi Yonatani mwana wake, komanso chifukwa cha anthu a Yehova ndi anthu a nyumba ya Isiraeli,+ amene anali atakanthidwa ndi lupanga.

13 Ndiyeno Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Kodi kwanu n’kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wa Mwamaleki, mlendo wokhala pakati pa Aisiraeli.”+ 14 Pamenepo Davide anati: “Zinatheka bwanji iwe osaopa+ kutambasula dzanja lako ndi kukantha wodzozedwa+ wa Yehova?” 15 Atatero, Davide anaitana mmodzi mwa anyamata ake ndi kumuuza kuti: “Mukanthe.” Chotero anamukanthadi, moti anafa.+ 16 Kenako Davide anamuuza kuti: “Mlandu wa magazi ako ukhale pamutu pako,+ chifukwa wadzichitira wekha umboni+ ponena kuti, ‘Ineyo ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”+

17 Ndiyeno Davide anayamba kuimba nyimbo iyi yoimba polira,+ pamene anali kulira Sauli ndi Yonatani mwana wake.+ 18 Iye ananenanso kuti, ana a Yuda+ aphunzitsidwe nyimboyi, yotchedwa “Uta.”+ Nyimbo imeneyi inalembedwa m’buku la Yasari:+

19 “Isiraeli iwe, anthu ako aulemerero aphedwa pamalo ako okwezeka.+

Haa! Anthu amphamvu agwa.

20 Anthu inu musanene zimenezi mumzinda wa Gati.+

Musalengeze zimenezi m’misewu ya Asikeloni,+

Kuopera kuti ana aakazi a Afilisiti angasangalale,+

Kuopera kuti ana aakazi a anthu osadulidwa angakondwere.

21 Inu mapiri a Giliboa,+ musalole kuti mame kapena mvula igwe pa inu. Musalole kuti minda imene ili pa inu ibale zipatso zokaperekedwa kwa Mulungu.*+

Chifukwa pa inu chishango cha amuna amphamvu chinadetsedwa,

Chishango cha Sauli, moti palibenso chishango chimene chinadzozedwa ndi mafuta.+

22 Uta wa Yonatani sunkalephera kupha adani ndi kukhetsa magazi awo,

Sunkalephera kubaya mafuta a anthu amphamvu.+

Lupanga la Sauli silinkabwerako chabe osakwaniritsa ntchito yake.+

23 Sauli ndi Yonatani,+ anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo,

Ngakhale pa imfa yawo sanasiyane.+

Iwo anali aliwiro kuposa chiwombankhanga,+

Amphamvu kuposa mikango.+

24 Ana aakazi a Isiraeli inu, mulirireni Sauli,

Amene anakuvekani zovala zamtengo wapatali* ndi zinthu zokongoletsa,

Amene anaika zokongoletsa zagolide pazovala zanu.+

25 Haa! Anthu amphamvu agwa pa nkhondo.+

Yonatani waphedwa pamalo anu okwezeka!+

26 Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe m’bale wanga Yonatani,

Unali wosangalatsa kwambiri kwa ine.+

Chikondi chako chinali chapamwamba kwambiri kuposa chikondi cha akazi.+

27 Haa! Anthu amphamvu agwa,+

Ndipo zida zankhondo zawonongeka.”

2 Ndiyeno pambuyo pake, Davide anayamba kufunsira kwa Yehova,+ kuti: “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Pita.” Davide anafunsanso kuti: “Ndipite kuti?” Iye anamuyankha kuti: “Ku Heburoni.”+ 2 Chotero Davide anapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala. 3 Davide anapitanso ndi amuna+ amene anali kuyenda naye, aliyense ndi banja lake. Iwo anakakhala m’mizinda ya m’dera la Heburoni. 4 Kenako amuna a ku Yuda+ anabwera ndi kudzoza+ Davide kumeneko kukhala mfumu ya nyumba ya Yuda.+

Ndiyeno anthu anauza Davide kuti: “Anthu a ku Yabesi-giliyadi ndi amene anaika Sauli m’manda.” 5 Choncho Davide anatumiza mithenga kwa amuna a ku Yabesi-giliyadi+ kuti akawauze kuti: “Yehova akudalitseni,+ chifukwa munasonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa mbuye wanu Sauli mwa kumuika m’manda.+ 6 Chotero Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ndipo muone kukhulupirika kwake. Inenso ndikusonyezani ubwino umenewu chifukwa mwachita zimenezi.+ 7 Tsopano manja anu alimbe ndipo mukhale amuna olimba mtima,+ chifukwa mbuye wanu Sauli wamwalira ndipo anthu a nyumba ya Yuda adzoza ine kukhala mfumu+ yawo.”

8 Ndiyeno Abineri+ mwana wa Nera, amene anali mtsogoleri wa asilikali a Sauli, anatenga Isi-boseti+ mwana wa Sauli ndi kuwolokera naye ku Mahanaimu.+ 9 Kumeneko anamulonga ufumu kuti azilamulira Giliyadi,+ Aasere, Yezereeli,+ Efuraimu+ ndi Benjamini,+ Isiraeli yense. 10 Isi-boseti mwana wa Sauli anali ndi zaka 40 pamene anakhala mfumu ya Isiraeli, ndipo analamulira zaka ziwiri. Anthu a nyumba ya Yuda+ okha ndi amene anali kutsatira Davide. 11 Nthawi yonse imene Davide anakhala mfumu ku Heburoni, kulamulira nyumba ya Yuda, inali zaka 7 ndi miyezi 6.+

12 Patapita nthawi, Abineri mwana wa Nera ndi atumiki a Isi-boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu+ n’kupita ku Gibeoni.+ 13 Nayenso Yowabu+ mwana wa Zeruya+ ndi atumiki a Davide, anapita kudziwe la Gibeoni ndipo magulu awiriwo anakumana kumeneko. Gulu la Yowabu linangokhala pansi kumbali ina ya dziwe ndipo gulu linalo linakhalanso kumbali inayo. 14 Pamapeto pake Abineri anauza Yowabu kuti: “Bwanji anyamata athu anyamuke ndipo amenyane tione.” Poyankha, Yowabu anati: “Chabwino, zitero.” 15 Chotero iwo ananyamuka. Kumbali ya Benjamini ndi Isi-boseti,+ mwana wa Sauli, anasankha anyamata 12, ndipo kwa atumiki a Davide anasankhanso anyamata 12. 16 Aliyense wa anyamatawo anagwira mnzake kumutu ndipo onse anabayana ndi lupanga m’mimba, moti onsewo anagwa pansi ndi kufa. Malo amenewo anatchedwa dzina lakuti Helikati-hazurimu,* ndipo ali ku Gibeoni.+

17 Pa tsiku limenelo, kumenyana kunakula ndipo kunali koopsa kwambiri. Pamapeto pake, Abineri+ ndi amuna a Isiraeli anagonjetsedwa ndi atumiki a Davide. 18 Ndiyeno ana atatu aamuna a Zeruya,+ amene ndi Yowabu,+ Abisai,+ ndi Asaheli+ anali pamenepo. Asaheli anali waliwiro kwambiri ngati mbawala+ yothamanga m’thengo. 19 Asaheliyo anayamba kuthamangitsa Abineri. Iye sanafune kutembenukira kudzanja lamanja kapena lamanzere pamene anali kutsatira Abineri. 20 Atamuthamangitsa kwa kanthawi ndithu, Abineri anayang’ana kumbuyo ndi kunena kuti: “Kodi ndiwe Asaheli?” Poyankha, Asaheli anati: “Ndine.” 21 Pamenepo Abineri anamuuza kuti: “Tembenukira kudzanja lako lamanja kapena lamanzere ndipo ugwire mmodzi mwa anyamatawo, kuti utenge zimene ungamuvule+ zikhale zako.” Koma Asaheli sanafune kutembenuka ndi kusiya kumutsatira. 22 Kenako Abineri anauzanso Asaheli kuti: “Tembenuka ndipo usiye kunditsatira, chifukwa ndingakuphe.+ Tsopano ndikakupha ndidzaonana bwanji ndi m’bale wako Yowabu?” 23 Koma Asaheli anakanabe kutembenukira kwina. Choncho Abineri anamubaya* pamimba+ ndi chogwirira cha mkondo, ndipo mkondowo unatulukira kumsana kwake, moti anagwa pansi n’kufera pomwepo. Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, aliyense wofika pamalo amene Asaheli anagwera ndi kufa, anali kuima chilili+ ndi kudabwa kwambiri.

24 Zitatero, Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri. Pamene dzuwa linali kulowa, iwo anafika paphiri la Ama, limene lili pafupi ndi Giya panjira yopita kuchipululu cha Gibeoni.+ 25 Ana a Benjamini anayamba kusonkhana kumbuyo kwa Abineri monga gulu limodzi. Iwo anaimabe pamwamba paphiri limodzi. 26 Pamenepo Abineri anayamba kufuulira Yowabu kuti: “Kodi tipitiriza kuphana ndi lupanga mpaka liti?+ Kodi sukudziwa kuti mapeto ake zimenezi zibweretsa mavuto aakulu?+ Kodi uwauza liti anthuwa kuti atembenuke ndi kusiya kutsatira abale awo?”+ 27 Poyankha, Yowabu anati: “Pali Mulungu woona wamoyo,+ ukanapanda kulankhula,+ anthuwa sakanatembenuka aliyense wa iwo kusiya kutsatira m’bale wake kufikira m’mawa.” 28 Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa,+ ndipo anthu onse anaima, moti sanapitirizenso kuthamangitsa Isiraeli. Iwo sanayambirenso kumenyana.

29 Abineri ndi amuna amene anali kuyenda naye anayenda kudutsa ku Araba+ usiku wonse mpaka anakawoloka Yorodano.+ Iwo anayenda kudutsa chigwa chonsecho ndi kukafika ku Mahanaimu.+ 30 Chotero Yowabu anasiya kutsatira Abineri ndipo anayamba kusonkhanitsa anthu onse pamodzi. Pagulu la atumiki a Davide panasowa amuna 19 komanso Asaheli. 31 Koma atumiki a Davidewo anali atakantha amuna a Benjamini ndi amuna ena a Abineri, moti amuna 360 anafa.+ 32 Iwo ananyamula mtembo wa Asaheli+ ndi kukauika m’manda a bambo ake+ ku Betelehemu.+ Kenako Yowabu ndi amuna amene anali kuyenda naye anayenda usiku wonse, ndipo kunawachera atafika ku Heburoni.+

3 Nkhondo ya pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide inatenga nthawi yaitali.+ Davide anapitirizabe kukhala wamphamvu+ koma nyumba ya Sauli inali kufookerafookera.+

2 Pa nthawiyi, Davide anabereka ana aamuna+ ku Heburoni,+ ndipo mwana wake woyamba anali Aminoni+ wobadwa kwa Ahinowamu+ wa ku Yezereeli. 3 Mwana wake wachiwiri anali Kileyabu+ wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala, ndipo wachitatu anali Abisalomu+ wobadwa kwa Maaka, mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya ku Gesuri. 4 Wachinayi anali Adoniya+ wobadwa kwa Hagiti,+ ndipo wachisanu anali Sefatiya+ wobadwa kwa Abitali. 5 Wa 6 anali Itireamu+ wobadwa kwa Egila, mkazi wa Davide. Amenewa ndi ana amene Davide anabereka ali ku Heburoni.

6 Ndiyeno pamene nkhondo ya pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide inali kupitirira, Abineri+ nayenso anali kukula mphamvu m’nyumba ya Sauli. 7 Tsopano Sauli anali ndi mdzakazi, dzina lake Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya.+ Patapita nthawi, Isi-boseti+ anafunsa Abineri kuti: “N’chifukwa chiyani unagona ndi mdzakazi*+ wa bambo anga?” 8 Abineri atamva mawu amenewa a Isi-boseti anakwiya kwambiri+ n’kunena kuti: “Kodi ine ndine galu+ wopanda pake wa Yuda? Ineyo ndikusonyeza kukoma mtima kosatha ku nyumba ya Sauli bambo ako, abale ake ndi mabwenzi ake apamtima, ndipo ndikukuteteza kuti usagwe m’manja mwa Davide, koma lero ukundiimba mlandu wa cholakwa chokhudza mkazi. 9 Mulungu alange ine Abineri mowirikiza,+ ngati sindidzachitira Sauli mogwirizana ndi zimene Yehova analumbira kwa Davide,+ 10 ndi kusamutsa ufumu kuuchotsa m’nyumba ya Sauli, n’kukhazikitsa mpando wachifumu wa Davide mu Isiraeli ndi mu Yuda, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.”+ 11 Pamenepo Isi-boseti sanathe kuyankha Abineri ngakhale liwu limodzi chifukwa anali kumuopa.+

12 Chotero, Abineri anatumiza mithenga kwa Davide nthawi yomweyo, kuti akamuuze kuti: “Kodi mwini dziko ndani?” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Chita nane pangano, ndipo inetu ndidzakuthandiza kutembenuza Isiraeli yense kukhala kumbali yako.”+ 13 Davide anamuyankha kuti: “Chabwino! Ineyo ndichitadi nawe pangano. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi ichi, ‘Usadzaone nkhope yanga+ pokhapokha utabweretsa Mikala,+ mwana wamkazi wa Sauli pobwera kuno.’” 14 Davide anatumizanso mithenga kwa Isi-boseti+ mwana wa Sauli ndi uthenga wonena kuti: “Ndipatse mkazi wanga Mikala, amene ndinalonjeza kumukwatira mwa kupereka makungu 100 akunsonga+ a Afilisiti.” 15 Choncho Isi-boseti anatuma anthu kuti akatenge Mikala kwa mwamuna wake Palitiyeli,*+ mwana wa Laisi. 16 Koma mwamuna wake anali kumutsatira. Iye anali kumutsatira pambuyo akulira mpaka kukafika ku Bahurimu.+ Kenako Abineri anamuuza kuti: “Bwerera!” Pamenepo iye anabwerera.

17 Izi zili choncho, Abineri analankhulana ndi akulu a Isiraeli kuti: “Kwa nthawi yaitali,+ mwakhala mukufuna Davide kuti akhale mfumu yanu. 18 Tsopano chitanipo kanthu, pakuti Yehova anauza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisiraeli m’manja mwa Afilisiti ndiponso m’manja mwa adani awo onse pogwiritsa ntchito dzanja la Davide+ mtumiki wanga.’” 19 Abineri analankhulanso ndi Abenjamini,+ kenako anapita kukauza Davide ku Heburoni zinthu zonse zimene zinali zabwino kwa Isiraeli ndi ku nyumba yonse ya Benjamini.

20 Abineri atafika kwa Davide ku Heburoni pamodzi ndi amuna 20, Davide anakonzera phwando+ Abineri ndi amuna amene anali naye. 21 Kenako Abineri anauza Davide kuti: “Ndiloleni ndinyamuke ndi kupita kuti ndikasonkhanitse Isiraeli yense kwa mbuyanga mfumu, kuti anthuwo achite pangano ndi inu ndipo mudzakhaladi mfumu pa zonse zimene moyo wanu umalakalaka.”+ Pamenepo Davide analola Abineri kupita ndipo ananyamukadi mwamtendere.+

22 Tsopano atumiki a Davide ndi Yowabu, anali kuchokera kunkhondo, atafunkha+ zinthu zambiri. Koma Abineri sanali ndi Davide ku Heburoni popeza anali atanyamuka mwamtendere ndipo anali pa ulendo wake. 23 Ndiyeno Yowabu+ anafika pamodzi ndi gulu lankhondo limene anali nalo, ndipo anthu anauza Yowabu kuti: “Abineri+ mwana wa Nera+ anafika kwa mfumu, ndipo mfumu yamulola kupita moti ali pa ulendo wake mwamtendere.” 24 Pamenepo Yowabu anapita kwa mfumu n’kunena kuti: “N’chiyani chimene mwachitachi?+ Abineri anabwera kwa inu. N’chifukwa chiyani mwamulola kuti anyamuke ndi kupita mwamtendere? 25 Inu mukum’dziwa bwino Abineri mwana wa Nera. Iye anabwera kuno kudzakupusitsani kuti adziwe kutuluka ndi kulowa kwanu,+ ndiponso kuti adziwe chilichonse chimene mukuchita.”+

26 Atanena mawu amenewa, Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza mithenga kuti itsatire Abineri. Mithengayo inabweza Abineri+ pachitsime cha Sira, koma Davide sanadziwe kena kalikonse. 27 Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anam’tengera pambali kuchipata kuti alankhulane naye pa awiri.+ Koma kumeneko anamubaya pamimba+ moti anafa chifukwa chokhetsa magazi a Asaheli,+ m’bale wake wa Yowabu. 28 Davide atamva zimenezi pambuyo pake, ananena kuti: “Pamaso pa Yehova, ineyo ndi ufumu wanga, mlandu wa magazi+ a Abineri mwana wa Nera sukutikhudza mpaka kalekale.* 29 Mlandu umenewu ubwerere pamutu+ pa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya bambo ake. M’nyumba ya Yowabu+ simudzasowa munthu wa nthenda yakukha kumaliseche+ ndiponso wakhate.+ Simudzasowanso mwamuna wogwira ndodo yowombera nsalu,+ wokanthidwa ndi lupanga kapena wosowa mkate!”+ 30 Yowabu ndi m’bale wake Abisai,+ anapha Abineri+ chifukwa chakuti iye anapha Asaheli m’bale wawo pa nkhondo ku Gibeoni.+

31 Ndiyeno Davide anauza Yowabu ndi anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Ng’ambani zovala zanu+ ndipo muvale ziguduli*+ kuti mulire maliro a Abineri.” Ngakhale Mfumu Davide nayenso anayenda pambuyo pa chithatha cha Abineri. 32 Choncho Abineri anamuika m’manda ku Heburoni. Ali kumandako, mfumu inayamba kulira mokweza mawu ndipo anthu onse anayambanso kulira.+ 33 Zitatero, mfumu inayamba kuimba nyimbo yolira Abineri kuti:

“Kodi zoona Abineri afe imfa ngati ya munthu wopanda pake?+

34 Manja ako sanali omangidwa,+

Ndipo mapazi ako sanaikidwe m’matangadza amkuwa.+

Wagwa ngati munthu wogwa pamaso pa anthu osalungama.”+

Pamenepo anthu onse anamuliranso.+

35 Pambuyo pake, anthu onse anabwera kwa Davide tsiku lomwelo kudzam’patsa chakudya+ chomutonthoza, koma Davide analumbira kuti: “Mulungu andilange+ mowirikiza ngati ndidzalawa chakudya kapena kena kalikonse dzuwa lisanalowe!”+ 36 Anthu onse anaona zimene zachitika, ndipo anaona kuti zimene mfumu ikuchita zili bwino. Mofanana ndi zonse zimene mfumuyo inachita, anthu onse anaona kuti izinso zili bwino.+ 37 Anthu onse a Davide komanso Isiraeli yense anadziwa tsiku limenelo kuti si mfumu imene inachititsa kuti Abineri mwana wa Nera aphedwe.+ 38 Ndiyeno mfumu inapitiriza kuuza atumiki ake kuti: “Kodi simukudziwa kuti amene wafa leroyu ndi kalonga komanso munthu wamphamvu mu Isiraeli?+ 39 Ine lero ndafooka ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa,+ ndipo ine ndikuona kuti amuna awa, ana a Zeruya,+ achita nkhanza kwambiri.+ Yehova abwezere aliyense wochita zinthu zoipa mogwirizana ndi kuipa kwake.”+

4 Mwana+ wa Sauli atamva kuti Abineri wafa ku Heburoni,+ manja ake analefuka+ ndipo Aisiraeli onse anasokonezeka. 2 Panali amuna awiri, atsogoleri a magulu a achifwamba+ a mwana wa Sauli. Mmodzi dzina lake anali Bana ndipo wina dzina lake anali Rekabu. Onsewa anali ana a Rimoni Mbeeroti+ wa fuko la Benjamini, pakuti dera la Beeroti nalonso linali kuonedwa ngati gawo la fuko la Benjamini. 3 Ndiyeno anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu,+ ndipo akhala kumeneko monga alendo mpaka lero.

4 Yonatani+ mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna wolumala mapazi.+ Mwanayu anali ndi zaka zisanu pamene kunabwera uthenga wa imfa ya Sauli ndi Yonatani kuchokera ku Yezereeli.+ Uthengawu utafika, mlezi wake anamunyamula ndi kuthawa naye. Pamene anali kuthawa mwamantha, mleziyo anagwetsa mwanayo ndipo analumala. Mwanayo dzina lake anali Mefiboseti.+

5 Rekabu ndi Bana, ana aamuna a Rimoni Mbeeroti, ananyamuka kupita kunyumba ya Isi-boseti+ masana kutatentha, ndipo anamupeza akugona. 6 Iwo analowa m’nyumbamo ngati anthu ofuna tirigu, kenako anakantha Isi-boseti pamimba.+ Atatero, Rekabu ndi m’bale wake Bana+ anathawa kuti asadziwike. 7 Iwo atalowa m’nyumbamo, anapeza Isi-boseti atagona pabedi m’chipinda chake, ndipo anamukantha ndi kumupha.+ Kenako anamudula mutu+ ndipo anautenga ndi kuyenda nawo usiku wonse mumsewu wopita ku Araba. 8 Kenako mutu wa Isi-boseti+ uja anafika nawo kwa Davide ku Heburoni ndi kuuza mfumuyo kuti: “Nawu mutu wa Isi-boseti mwana wa mdani wanu Sauli,+ amene anali kufunafuna moyo wanu.+ Lero Yehova wabwezera+ Sauli ndi mbadwa zake chifukwa cha inu mbuyanga mfumu.”

9 Koma Davide anayankha Rekabu ndi m’bale wake Bana, ana a Rimoni Mbeeroti kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ amene anawombola+ moyo wanga+ m’masautso anga onse,+ 10 pamene munthu wina anandibweretsera uthenga+ wakuti, ‘Sauli wafa,’ ndipo iye anali kuganiza kuti wabweretsa uthenga wabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha+ ku Zikilaga m’malo momulipira monga mthenga. 11 Ndiye kuli bwanji pamene anthu oipa+ apha munthu wolungama pabedi m’nyumba yake? Kodi sindiyenera kufuna magazi ake m’manja mwanu+ ndi kukuchotsani padziko?”+ 12 Pamenepo Davide analamula anyamata ake ndipo anapha Rekabu ndi Bana+ ndipo anadula manja ndi mapazi awo. Kenako anawapachika+ pafupi ndi dziwe la ku Heburoni, koma anatenga mutu wa Isi-boseti ndi kuuika m’manda a Abineri ku Heburoni.+

5 Patapita nthawi, mafuko onse a Isiraeli anapita kwa Davide+ ku Heburoni+ ndi kumuuza kuti: “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.+ 2 Kuyambira kale+ pamene Sauli anali mfumu yathu, inuyo munali kutsogolera Isiraeli polowa ndi potuluka.+ Ndipo Yehova anakuuzani kuti, ‘Udzaweta+ anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri+ wa Isiraeli.’” 3 Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+

4 Davide anali ndi zaka 30 pamene anakhala mfumu. Iye analamulira monga mfumu kwa zaka 40.+ 5 Ku Heburoni analamulira monga mfumu ya Yuda zaka 7 ndi miyezi 6.+ Ku Yerusalemu+ analamulira monga mfumu ya Isiraeli yense ndiponso Yuda zaka 33. 6 Patapita nthawi, mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene anali kukhala kumeneko. Ayebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno, pakuti upitikitsidwa ndi anthu akhungu ndi olumala.”+ Mumtima mwawo iwo anali kunena kuti: “Davide sangalowe mumzinda uno.” 7 Ngakhale zinali choncho, Davide analanda Ziyoni, malo okhala mumpanda wolimba kwambiri,+ umene ndi Mzinda wa Davide.+ 8 Choncho Davide pa tsiku limenelo anati: “Aliyense wofuna kukaukira Ayebusi+ adutse m’ngalande zamadzi+ ndi kukakumana ndi anthu olumala ndi akhungu, anthu amene ine Davide ndimadana nawo kwambiri!” N’chifukwa chake pali mawu onena kuti: “Wakhungu ndi wolumala asalowe m’nyumba.” 9 Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati. 10 Chotero ulamuliro wa Davide unakulirakulira,+ ndipo Yehova Mulungu wa makamu+ anali naye.+

11 Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza amithenga+ kwa Davide. Anatumizanso mitengo ya mkungudza,+ anthu a ntchito zamatabwa ndi a ntchito za miyala yomangira khoma,* ndipo anayamba kumanga nyumba ya Davide.+ 12 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ komanso kuti wamukwezera+ ufumu wake chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+

13 Pambuyo pake, Davide anatenganso adzakazi+ ndi akazi+ ena mu Yerusalemu atachoka ku Heburoni, moti anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+ 15 Ibara, Elisua,+ Nefegi,+ Yafiya,+ 16 Elisama,+ Eliyada ndi Elifeleti.+

17 Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide. Davide atamva zimenezi, anakabisala kumalo ovuta kufikako.+ 18 Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 19 Ndiyeno Davide anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwapereka m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, ndipereka ndithu Afilisitiwa m’manja mwako.”+ 20 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula ndi kuwononga adani anga.”+ N’chifukwa chake malowo anawatcha Baala-perazimu.*+ 21 Pa nthawiyi, Afilisiti anasiya mafano awo+ kumeneko, choncho Davide ndi anthu ake anawatenga.+

22 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso+ ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 23 Pamenepo Davide anafunsira+ kwa Yehova ndipo anamuyankha kuti: “Ayi usapite. Koma uwazembere kumbuyo kwawo ndi kuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 24 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka, pamenepo ukachitepo kanthu mwachangu,+ chifukwa pa nthawiyo Yehova adzakhala atatsogola kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.”+ 25 Pamenepo Davide anachitadi momwemo, monga mmene Yehova anamulamulira,+ moti anapha+ Afilisiti kuchokera ku Geba*+ mpaka kukafika ku Gezeri.+

6 Davide anasonkhanitsanso amuna onse osankhidwa mwapadera mu Isiraeli,+ okwana 30,000. 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+ 3 Koma iwo anakweza likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo,+ ana aamuna a Abinadabu, anali kutsogolera ngolo yatsopanoyo.

4 Choncho ananyamula likasa la Mulungu woona kulichotsa kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri, ndipo Ahiyo anali kuyenda patsogolo pa Likasa. 5 Davide pamodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kusangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Anali kuimbanso zeze,+ zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana. 6 Kenako anafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, ndipo Uza+ anatambasulira dzanja lake pa likasa la Mulungu woona n’kuligwira,+ chifukwa ng’ombe zinatsala pang’ono kuligwetsa. 7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova+ unayakira Uza ndipo Mulungu woona anamukantha+ pomwepo chifukwa cha kuchita chinthu chosalemekeza Mulungu chimenechi. Moti Uza anafera pomwepo, pafupi ndi likasa la Mulungu woona.+ 8 Zitatero, Davide anakwiya chifukwa mkwiyo wa Yehova unaphulikira Uza modzidzimutsa. Chotero malo amenewo amatchedwa dzina lakuti Perezi-uza* kufikira lero.+ 9 Tsiku limenelo, Davide anachita mantha kwambiri chifukwa cha Yehova,+ ndipo anati: “Kodi likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10 Pamenepo Davide sanafunenso kutenga likasa la Yehova kupita nalo kumene iye anali kukhala, ku Mzinda wa Davide.+ Chotero Davide analipatutsira kunyumba ya Obedi-edomu+ Mgiti.+

11 Likasa la Yehova linakhalabe kunyumba ya Obedi-edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anapitiriza kudalitsa+ Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+ 12 Pamapeto pake uthenga unafika kwa Mfumu Davide wonena kuti: “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-edomu ndi zake zonse chifukwa cha likasa la Mulungu woona.” Davide atamva mawu amenewa anapita kukatenga likasa la Mulungu woona kunyumba kwa Obedi-edomu ndi kupita nalo ku Mzinda wa Davide, akusangalala.+ 13 Tsopano onyamula+ likasa la Yehova atangoyenda mapazi 6, nthawi yomweyo Davide anapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi chiweto chonenepa.+

14 Davide ankavina mozungulira pamaso pa Yehova ndi mphamvu zake zonse. Apa n’kuti Davide atavala efodi+ wansalu. 15 Davide ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kupita ndi likasa+ la Yehova, akufuula mokondwera+ ndi kuimba lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 16 Ndiyeno pamene likasa la Yehova linalowa mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kuvina mozungulira pamaso pa Yehova. Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.+ 17 Ndiyeno analowetsa likasa la Yehova muhema limene Davide anamanga n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako Davide anapereka kwa Yehova nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ 18 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova+ wa makamu. 19 Kuwonjezera apo, anthu onse, khamu lonse la Isiraeli, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira yoboola pakati, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi.+ Kenako aliyense wa anthuwo anapita kunyumba yake.

20 Tsopano Davide anabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake.+ Pamenepo Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kukakumana naye ndipo anati: “Lerotu mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake+ mwa kudzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, monga mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi ngakhale pang’ono!”+ 21 Poyankha, Davide anauza Mikala kuti: “Ine ndinali kusangalala pamaso pa Yehova amene anandisankha kuti ndikhale mtsogoleri+ wa anthu a Yehova, Aisiraeli, m’malo mwa bambo ako ndi banja lawo lonse, ndipo ndidzasangalala pamaso pa Yehova.+ 22 Ndipotu ndipitiriza kudzipeputsa kuposa pamenepa,+ moti ndidzichepetsa m’maso mwanga. Ndine wotsimikiza mtima kudzipezera ulemerero pamaso pa akapolo aakazi amene ukunenawo.”+ 23 Choncho Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli sanakhalepo ndi mwana mpaka tsiku la imfa yake.

7 Ndiyeno pamene mfumu inali kukhala m’nyumba yake,+ ndipo Yehova ataipatsa mpumulo kwa adani ake onse oizungulira,+ 2 inauza Natani+ mneneri kuti: “Tsopano taona, ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza,+ pamene likasa la Mulungu woona likukhala m’chihema chansalu.”+ 3 Pamenepo Natani anauza mfumu kuti: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu,+ chifukwa Yehova ali nanu.”

4 Tsopano usiku umenewo, Yehova analankhula+ ndi Natani, kuti: 5 “Pita, ukauze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwe ungandimangire nyumba yoti ine ndikhalemo?+ 6 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa ana a Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba koma nthawi zonse ndinali kuyenda+ m’chihema chopatulika.+ 7 Pa nthawi yonse imene ndinali kuyendayenda pakati pa ana a Isiraeli onse,+ kodi ndinalankhulapo mawu ndi limodzi mwa mafuko onse a Isiraeli,+ fuko limene ndinalilamula kutsogolera anthu anga Aisiraeli, kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu inu simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’ 8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa, kumene unali kusamalira nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli. 9 Ine ndidzakhala ndi iwe kulikonse kumene udzapite,+ ndipo ndidzawononga ndi kuchotsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzakupangira dzina lotchuka,+ lofanana ndi dzina la anthu otchuka amene ali m’dziko. 10 Ndipo anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo+ ndi kuwakhazika+ pamalowo. Iwo adzakhaladi kumeneko ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu osalungama sadzawasautsanso ngati mmene anachitira poyamba,+ 11 kuchokera tsiku limene ndinaika oweruza+ kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli. Ndidzakupatsa mpumulo kwa adani ako onse.+

“‘“Tsopano Yehova wakuuza kuti, Yehova adzakukhazikitsira banja lachifumu.+ 12 Masiku ako akadzakwana,+ ndipo ukadzagona pamodzi ndi makolo ako,+ pamenepo ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako, imene idzatuluka m’chiuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.+ 13 Iye ndi amene adzamangira dzina langa nyumba,+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 14 Ine ndidzakhala atate wake+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Akachita zoipa, ine ndidzam’dzudzula ndi ndodo+ ya anthu ndi zikoti za ana a Adamu. 15 Ndipo kukoma mtima kwanga kosatha sikudzachoka pa iye monga mmene ndinakuchotsera pa Sauli,+ amene ndinam’chotsa pamaso pako. 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikika pamaso pako mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+

17 Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+

18 Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova, ndipo inati: “Ndine yani ine,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? Ndipo nyumba yanga n’chiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano? 19 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, kuwonjezeranso pamenepa, mwangondiuza kumene kuti nyumba ya mtumiki wanu idzakhazikika mpaka m’tsogolo kwambiri. Limenelitu ndi lamulo limene mwapereka kwa anthu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ 20 Ndiyeno ine Davide ndinganenenji kuwonjezera pa zimene inu mwanena, pamene ndinu amene mukundidziwa bwino ine mtumiki wanu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? 21 Inu mwachita zazikulu zonsezi monga mwa mawu anu,+ komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,+ ndipo mwandidziwitsa ine mtumiki wanu.+ 22 N’chifukwa chake ndinudi wokwezeka,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Ngakhale kuti tamva za milungu ina yambirimbiri, palibe Mulungu wina+ koma inu nokha.+ 23 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu munawawombola monga anthu anu+ ndi kudzipangira dzina,+ amene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha?+ Munapitikitsa mitundu ina ndi milungu yawo, chifukwa cha anthu anu amene munawawombola+ nokha kuchokera ku Iguputo. 24 Inutu munadzikhazikitsira anthu anu Aisiraeli+ kuti akhaledi anthu anu mpaka kalekale. Ndipo inu Yehova mwakhala Mulungu wawo.+

25 “Tsopano inu Yehova Mulungu, chitani mpaka kalekale mawu amene mwalankhula okhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake. Chitani mmene mwanenera.+ 26 Dzina lanu likwezeke mpaka kalekale.+ Anthu anene kuti, ‘Yehova wa makamu ndi Mulungu wa Isiraeli,’+ ndipo nyumba ya mtumiki wanu Davide ikhazikike pamaso panu.+ 27 Pakuti inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, mwaululira ine mtumiki wanu kuti, ‘Ndidzakumangira nyumba.’*+ N’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera kwa inu pemphero lino.+ 28 Tsopano inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu Mulungu woona. Kunena za mawu anu, akhale oona,+ pakuti mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+ 29 Choncho dalitsani+ nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Pakuti inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa mwalonjeza, ndipo madalitso anu akhale panyumba ya mtumiki wanu mpaka kalekale.”+

8 Pambuyo pake, Davide anapha Afilisiti+ ndi kuwagonjetsa,+ ndipo anawalanda mzinda wa Metege-ama.

2 Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndi kuwayeza ndi chingwe. Iye anawagoneka pansi kuti ayeze zingwe ziwiri ndi kuwapha, ndiponso chingwe chimodzi chathunthu n’kuwasiya amoyo.+ Choncho Amowabu anakhala atumiki a Davide+ ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+

3 Davide anapha Hadadezeri,+ mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukabwezeretsa ulamuliro wake kumeneko. 4 Davide anagwira amuna 1,700 okwera pamahatchi ndi amuna 20,000 oyenda pansi+ a Hadadezeri. Kenako Davide anapundula*+ mahatchi onse a magaleta+ kusiyapo mahatchi a magaleta okwana 100.

5 Pamene Asiriya a ku Damasiko+ anabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anapha amuna 22,000 a ku Siriya.+ 6 Kenako Davide anamanga midzi ya asilikali+ m’dera la Asiriya a ku Damasiko ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho+ kwa iye. Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene wapita.+ 7 Komanso Davide anatenga zishango zozungulira+ zagolide zimene zinali ndi atumiki a Hadadezeri ndipo anabwera nazo ku Yerusalemu. 8 Mfumu Davide inatenga mkuwa wochuluka kwambiri+ ku Beta ndi Berota, mizinda ya Hadadezeri.

9 Tsopano Toi, mfumu ya Hamati+ anamva kuti Davide wapha gulu lonse lankhondo la Hadadezeri.+ 10 Choncho Toi anatumiza Yoramu mwana wake kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake+ ndi kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri ndi kumugonjetsa (pakuti Hadadezeri ndi Toi anali kumenyana kawirikawiri). Popita kwa Davide, Yoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.+ 11 Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide wochokera ku mitundu yonse imene inagonjetsa.+ 12 Inapatula siliva ndi golide wochokera ku Siriya, Mowabu,+ kwa ana a Amoni, Afilisiti,+ Aamaleki+ ndiponso siliva ndi golide amene anafunkha kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba.+ 13 Ndipo Davide anadzipangira dzina atabwerako kumene anapha Aedomu 18,000+ m’chigwa cha Mchere.+ 14 Davide anakhazikitsa midzi ya asilikali mu Edomu.+ Mu Edomu yense anaikamo midzi ya asilikali, moti Aedomu anakhala antchito a Davide+ ndipo Yehova anali kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+

15 Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli+ yense ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo+ kwa anthu ake onse.+ 16 Yowabu+ mwana wa Zeruya anali mkulu wa asilikali, ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 17 Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara anali ansembe, pamene Seraya anali mlembi. 18 Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti.+ Ana aamuna a Davide anakhala ansembe.*+

9 Ndiyeno Davide ananena kuti: “Kodi pali aliyense wotsala wa m’nyumba ya Sauli? Ndikufuna kumusonyeza kukoma mtima kosatha+ chifukwa cha Yonatani.”+ 2 Tsopano nyumba ya Sauli inali ndi mtumiki, dzina lake Ziba.+ Choncho anamuitanira kwa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Ziba?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndine mtumiki wanu.” 3 Ndiyeno mfumu inati: “Kodi palibe aliyense wotsala m’nyumba ya Sauli? Ndikufuna kumusonyeza kukoma mtima kosatha kwa Mulungu.”+ Poyankha Ziba anauza mfumu kuti: “Alipo mwana wamwamuna wa Yonatani, wolumala mapazi.”+ 4 Pamenepo mfumu inamufunsa kuti: “Ali kuti?” Ziba anayankha mfumu kuti: “Ali m’nyumba ya Makiri,+ mwana wamwamuna wa Amiyeli, ku Lo-debara.”+

5 Nthawi yomweyo Mfumu Davide anatumiza anthu kuti akamutenge kunyumba ya Makiri, mwana wa Amiyeli, ku Lo-debara. 6 Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, atalowa ndi kuonana ndi Davide, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ Pamenepo Davide anati: “Mefiboseti!” Poyankha, iye anati: “Ndine pano mtumiki wanu.” 7 Ndiyeno Davide anamuuza kuti: “Usaope. Ndithu, ndikusonyeza kukoma mtima kosatha+ chifukwa cha Yonatani bambo ako.+ Ndikubwezera munda wonse+ wa Sauli agogo ako ndipo iweyo uzidya mkate patebulo langa nthawi zonse.”+

8 Mefiboseti atamva zimenezi anawerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndine ndani kuti mukumbukire galu wakufa+ ngati ine?” 9 Ndiyeno mfumu inaitana Ziba, mtumiki wa Sauli, ndi kumuuza kuti: “Chilichonse chimene chinali cha Sauli komanso chilichonse cha m’nyumba yake yonse, ine ndikupereka+ kwa mdzukulu wa mbuye wako. 10 Iweyo, ana ako aamuna ndi antchito ako, muzimulimira munda wake ndi kumukololera kuti anthu a m’nyumba ya mdzukulu wa mbuye wako azikhala ndi chakudya chimene azidya. Koma Mefiboseti, mdzukulu wa mbuye wako, azidya chakudya patebulo langa nthawi zonse.”+

Tsopano Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi antchito 20.+ 11 Pamenepo Ziba anayankha mfumu kuti: “Zonse zimene mbuyanga mfumu yanena kwa ine mtumiki wanu ndichita zomwezo, koma Mefiboseti+ akudya patebulo langa* ngati mmodzi wa ana a mfumu.” 12 Tsopano Mefiboseti anali ndi mwana wamng’ono wamwamuna dzina lake Mika,+ ndipo anthu onse okhala m’nyumba ya Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13 Choncho Mefiboseti anali kukhala mu Yerusalemu pakuti anali kudya patebulo la mfumu nthawi zonse.+ Iye anali wolumala mapazi.+

10 Pambuyo pake, mfumu ya ana a Amoni+ inamwalira, ndipo Hanuni mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwa bambo ake.+ 2 Zitachitika zimenezi, Davide anati: “Ndidzasonyeza Hanuni mwana wa Nahasi kukoma mtima kosatha,+ monga mmene bambo ake anandisonyezera kukoma mtima kosatha.” Chotero Davide anatumiza uthenga kudzera mwa atumiki ake+ kuti akatonthoze Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo ake, ndipo atumiki a Davidewo anafika m’dziko la ana a Amoni. 3 Koma akalonga a ana a Amoni anauza Hanuni mbuye wawo kuti: “Kodi ukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthoza kuti alemekeze bambo ako pamaso pako? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kwa iwe kuti adzaonetsetse mzindawu ndi kuchita ukazitape,+ kuti adzaulande?”+ 4 Pamenepo Hanuni anatenga atumiki a Davide aja ndi kuwameta ndevu zonse za mbali imodzi,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza m’matako, n’kuwauza kuti azipita.+ 5 Pambuyo pake anthu anauza Davide zimene zinachitika, ndipo iye nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane ndi atumiki akewo chifukwa atumikiwo anaona kuti awachititsa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ kufikira ndevu zanu zitachuluka ndithu, kenako mudzabwere.”

6 Patapita nthawi, ana a Amoni anaona kuti akhala chinthu chonunkha+ kwa Davide. Choncho anatumiza nthumwi kuti akalembe ganyu Asiriya a ku Beti-rehobu+ ndi Asiriya a ku Zoba,+ amuna 20,000 oyenda pansi. Anapitanso kwa mfumu ya ku Maaka+ ndi kulemba ganyu amuna 1,000 ndi ku Isitobu amuna 12,000. 7 Davide atamva zimenezi anatumiza Yowabu ndi gulu lonse lankhondo pamodzi ndi amuna amphamvu.+ 8 Ndiyeno ana a Amoni anapita kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuchipata cha mzinda. Nawonso Asiriya a ku Zoba, a ku Rehobu,+ a ku Isitobu ndi a ku Maaka anafola paokha kutchire.+

9 Yowabu ataona kuti asilikali a adani ake akubwera mofulumira kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo kudzamenyana naye, nthawi yomweyo anatenga amuna ochita kusankhidwa mwapadera+ a mu Isiraeli ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti akumane ndi Asiriya. 10 Anthu ena onse anawapereka m’manja mwa Abisai+ m’bale wake, kuti awatsogolere pofola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi kukumana ndi ana a Amoni.+ 11 Ndiyeno anamuuza kuti: “Asiriya akandiposa mphamvu, iweyo undipulumutse. Koma ana a Amoni akakukulira mphamvu, ineyo ndifika kudzakupulumutsa.+ 12 Chita zinthu mwamphamvu, ndipo tisonyeze kulimba mtima+ chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu.+ Yehova adzachita zimene zili zabwino m’maso mwake.”+

13 Choncho Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya, moti Asiriya anathawa pamaso pake.+ 14 Pamenepo ana a Amoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa pamaso pa Abisai ndi kubwerera kwawo.+ Kenako Yowabu anasiya kutsatira ana a Amoni ndi kubwerera ku Yerusalemu.+

15 Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, anasonkhana pamodzi. 16 Choncho Hadadezeri+ anatumiza nthumwi kukatenga Asiriya amene anali m’dera la ku Mtsinje.*+ Atatero anabwera ku Helamu pamodzi ndi Sobaki+ mtsogoleri wa gulu lankhondo la Hadadezeri.

17 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse ndi kuwoloka Yorodano kupita ku Helamu. Ndiyeno Asiriya anafola kuti akumane ndi Davide ndi kuyamba kumenyana naye.+ 18 Asiriyawo anathawa+ pamaso pa Isiraeli, ndipo Davide anapha asilikali a Siriya 700 okwera magaleta,+ ndi asilikali 40,000 okwera pamahatchi. Iye anakanthanso Sobaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo la Siriya, moti anafera pomwepo.+ 19 Mafumu onse+ amene anali atumiki a Hadadezeri, ataona kuti agonja pamaso pa Isiraeli,+ nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Aisiraeli ndi kuyamba kuwatumikira.+ Asiriya sanayesenso kupulumutsa ana a Amoni chifukwa anali kuchita mantha.+

11 Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Davide anatumiza Yowabu, atumiki ake ndi Isiraeli yense kuti akawononge ana a Amoni+ ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.

2 Ndiyeno tsiku lina madzulo, Davide anadzuka pabedi lake, n’kupita kukayendayenda padenga*+ la nyumba yachifumu. Ali pamenepo anaona+ mkazi akusamba, ndipo mkaziyo anali wooneka bwino kwambiri.+ 3 Zitatero, Davide anatuma nthumwi kukafufuza za mkaziyo.+ Ndiyeno munthu wina ananena kuti: “Kodi ameneyu si Bati-seba+ mwana wa Eliyamu,*+ mkazi wa Uriya+ Mhiti?”+ 4 Kenako Davide anatuma nthumwi kuti akamutenge.+ Choncho mkaziyo anabweradi kwa Davide+ ndipo Davide anagona naye+ pa nthawi imene mkaziyo anali kudziyeretsa ku chodetsa chake.+ Zitatero mkaziyo anabwerera kunyumba yake.

5 Tsopano mkaziyo anakhala ndi pakati. Choncho anatumiza uthenga kwa Davide wonena kuti: “Ndili ndi pakati.” 6 Pamenepo Davide anatumiza uthenga kwa Yowabu wonena kuti: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Choncho Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide. 7 Uriya atafika kwa Davide, Davideyo anayamba kumufunsa za umoyo wa Yowabu, za umoyo wa anthu ndi mmene nkhondo inali kuyendera. 8 Pamapeto pake, Davide anauza Uriya kuti: “Pita kunyumba kwako ukasambe mapazi ako.”+ Uriya anatuluka m’nyumba ya mfumu ndipo pambuyo pake mfumuyo inamutumizira mphatso. 9 Koma Uriya anagona pakhomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi atumiki ena a mbuye wake, moti sanapite kunyumba yake. 10 Choncho anthu anauza Davide kuti: “Uriya sanapite kunyumba kwake.” Atamva zimenezi, Davide anauza Uriya kuti: “Iweyo wayenda ulendo wautali, si choncho kodi? Bwanji sunapite kunyumba kwako?” 11 Pamenepo Uriya anayankha Davide kuti: “Likasa,+ Isiraeli ndi Yuda akukhala m’misasa, ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi atumiki anu mbuyanga+ ali mumsasa kuthengo. Ndiye ine ndikalowe m’nyumba yanga kukadya chakudya, kumwa ndi kugona ndi mkazi wanga?+ Ndithu, pali inu ndi moyo wanu,+ sindingachite zimenezo.”

12 Ndiyeno Davide anauza Uriya kuti: “Leronso usanyamuke ndipo mawa ndikulola kupita.” Choncho Uriya anakhalabe ku Yerusalemu tsiku limenelo ndiponso tsiku lotsatira. 13 Kuwonjezera apo, Davide anamuitana kuti adye ndi kumwa naye pamodzi, ndipo anamuledzeretsa.+ Ngakhale zinali choncho, madzulo Uriya anapita kwa atumiki a mbuye wake kukagona pabedi, ndipo sanapite kunyumba kwake. 14 Ndiyeno m’mawa mwake, Davide analembera kalata+ Yowabu n’kupatsira Uriya. 15 M’kalatamo analembamo kuti:+ “Muike Uriya kutsogolo kumene nkhondo yakula,+ ndipo inu mubwerere m’mbuyo kuti amukanthe ndipo afe ndithu.”+

16 Pamene Yowabu anazungulira mzinda wa Raba, anaika Uriya pamalo amene anadziwa kuti akumana ndi amuna amphamvu.+ 17 Pamene amuna a mzindawo anatuluka kudzamenyana ndi Yowabu, ena mwa anthu, atumiki a Davide anakanthidwa ndi kugwa, ndipo Uriya Mhiti nayenso anafa.+ 18 Tsopano Yowabu anatumiza mthenga kuti akauze Davide zonse zimene zikuchitika kunkhondo. 19 Yowabu analamula mthengayo kuti: “Ukakangomaliza kufotokozera mfumu zonse zokhudza nkhondoyi, 20 ndiyeno mfumu n’kukwiya ndi kukufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mumamenya nkhondo moyandikira mzindawo kwambiri choncho? Kodi amuna inu simunali kudziwa kuti adzaponya mivi kuchokera pamwamba pa mpanda? 21 Ndani uja anapha Abimeleki+ mwana wa Yerubeseti?*+ Kodi si mkazi amene anaponya mwala wokhala pamwamba wa mphero+ ali pamwamba pa mpanda, ndipo Abimeleki anafera ku Tebezi+ komweko? N’chifukwa chiyani amuna inu munauyandikira kwambiri mpandawo?’ Pamenepo ukanene kuti, ‘Nayenso Uriya Mhiti, mtumiki wanu, wafa.’”+

22 Choncho mthengayo anapita, ndipo atafika kwa Davide anamuuza zonse zimene Yowabu anamutuma. 23 Ndiyeno mthengayo anauza Davide kuti: “Amunawo anakula mphamvu kuposa ife, moti anatuluka kudzamenyana nafe kuthengo, koma tinayesetsa kuwapanikiza mpaka kuchipata cha mzinda. 24 Koma oponya mivi anapitirizabe kulasa atumiki anu kuchokera pamwamba pa mpanda,+ moti ena mwa atumiki a mfumu afa. Nayenso Uriya Mhiti, mtumiki wanu wafa.”+ 25 Pamenepo Davide anauza mthengayo kuti: “Ukamuuze Yowabu kuti, ‘Usavutike mtima chifukwa cha nkhani imeneyi, pakuti lupanga lingakanthe+ wina aliyense. Inuyo menyani nkhondo mwamphamvu ndi mzindawo ndipo muugonjetse.’+ Choncho, ukamulimbikitse Yowabu.”

26 Pamenepo mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake+ wafa, ndipo anayamba kumulira.+ 27 Nyengo yolira maliro+ itatha, nthawi yomweyo Davide anatumiza nthumwi kukatenga Bati-seba ndi kubwera naye kunyumba kwake, ndipo anakhala mkazi wake.+ Patapita nthawi, anamuberekera mwana wamwamuna. Koma zimene Davide anachitazi zinamuipira kwambiri Yehova.+

12 Tsopano Yehova anatuma Natani+ kwa Davide. Natani atafika kwa Davide+ anamuuza kuti: “Panali amuna awiri amene anali kukhala mumzinda umodzi. Wina anali wolemera ndipo wina anali wosauka. 2 Munthu wolemera uja anali ndi nkhosa ndi ng’ombe zambiri.+ 3 Koma munthu wosauka uja anali ndi kamwana ka nkhosa kamodzi kokha kakakazi kamene anagula.+ Iye anali kusunga kamwana ka nkhosako ndipo kanali kukula pamodzi ndi ana ake. Munthuyo anali kudya ndi kumwa nako pamodzi ndipo kanali kugona pachifuwa chake. Kwa iye kanali ngati mwana wake wamkazi. 4 Patapita nthawi, kwa munthu wolemera uja kunabwera mlendo. Koma munthu wolemerayo sanatenge zina mwa nkhosa zake ndi ng’ombe zake kuti akonzere mlendo amene anabwera kwawoyo. M’malomwake, anatenga kamwana ka nkhosa kakakazi ka munthu wosauka uja ndi kukonzera munthu amene anabwera kwawoyo kuti adye.”+

5 Davide atamva zimenezi anamukwiyira kwambiri munthuyo,+ moti anauza Natani kuti: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ munthu wochita zimenezi ayenera kufa!+ 6 Ndiponso ayenera kubweza+ nkhosa zinayi+ chifukwa cha kamwana ka nkhosa kakakazi kamene anatenga. Amenewa ndiwo malipiro a zimene wachitazi, pakuti analibe chisoni.”+

7 Pamenepo Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyo ndiwe! Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndinakudzoza+ iwe kuti ukhale mfumu ya Isiraeli ndipo ndinakupulumutsa+ m’manja mwa Sauli. 8 Ine ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako+ ndi akazi a mbuye wako+ pachifuwa chako. Ndinakupatsanso nyumba ya Isiraeli ndi ya Yuda.+ Zinthu zimenezi zikanakhala kuti sizinakukwanire, ndinali wokonzeka kuziwonjezera ndiponso kukupatsa zinthu zina.+ 9 N’chifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova mwa kuchita chinthu choipa+ pamaso pake? Uriya Mhiti unamupha ndi lupanga, ndipo mkazi wake unamutenga kukhala mkazi wako,+ pamene Uriyayo unamupha ndi lupanga+ la ana a Amoni. 10 Tsopano lupanga+ silidzachoka panyumba yako mpaka kalekale.+ Chimenechi n’chotsatira cha zimene unachita chifukwa chondinyoza mwa kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala mkazi wako.’ 11 Ndiyeno Yehova wanena kuti, ‘Taona, ndikukugwetsera tsoka m’nyumba yako yomwe.+ Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa mwamuna wina,+ ndipo iye adzagona ndi akazi ako anthu onse akuona.+ 12 Iweyo unachita zinthu zimenezi mobisa,+ koma ine ndidzachita zimenezi pamaso pa Isiraeli+ yense, masanasana.’”+

13 Pamenepo Davide anauza+ Natani kuti: “Ndachimwira Yehova.”+ Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Yehova wakukhululukira tchimo lako+ ndipo suufa.+ 14 Ngakhale zili choncho, chifukwa chakuti wanyoza+ Yehova mwa kuchita zimenezi, mwana wako wamwamuna amene wangobadwa kumeneyu adzafa ndithu.”+

15 Kenako Natani anapita kunyumba kwake.

Ndiyeno Yehova anakantha+ mwana amene mkazi wa Uriya anaberekera Davide, moti mwanayo anayamba kudwala. 16 Zitatero Davide anayamba kuchonderera Mulungu woona chifukwa cha mwanayo, ndipo anasiyiratu kudya.+ Kenako Davide analowa m’nyumba ndipo usiku umenewo anagona pansi.+ 17 Ndiyeno akulu a m’nyumba yake anabwera pamene iye anagonapo kuti amudzutse. Koma iye sanalole ndipo sanadye chakudya+ pamodzi nawo. 18 Ndiyeno pa tsiku la 7, mwanayo anamwalira. Zitatero, atumiki a Davide anaopa kumuuza kuti mwana uja wamwalira, ndipo anali kunena kuti: “Pamenetu mwanayu anali ndi moyo tinalankhula naye Davide, koma sanatimvere. Ndiye tingamuuze bwanji kuti, ‘Mwana uja wamwalira’? Tikamuuza adzachita chinachake choipa.”

19 Davide ataona kuti atumiki ake akunong’onezana, anazindikira kuti mwana uja wamwalira. Choncho anafunsa atumiki akewo kuti: “Kodi mwana uja wamwalira?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde wamwalira.” 20 Davide atamva zimenezi anadzuka pansi pamene anagonapo n’kukasamba ndi kudzola+ mafuta. Kenako anasintha zovala zake n’kukalowa m’nyumba+ ya Yehova ndipo anagwada n’kuweramira pansi.+ Atachoka kumeneko anakalowa m’nyumba yake ndi kupempha kuti amukonzere chakudya. Mwamsanga anam’bweretsera mkate ndipo anadya. 21 Pamenepo atumiki ake anam’funsa kuti: “Kodi zimene mwachitazi zikutanthauza chiyani? Pamene mwana anali moyo, munali kukana chakudya ndipo munali kulira chifukwa cha mwanayo. Koma mwana atangomwalira, mwadzuka ndi kuyamba kudya mkate.” 22 Iye anayankha kuti: “Pamene mwana anali ndi moyo ndinali kusala kudya+ ndipo ndinali kulira+ chifukwa mumtima mwanga ndinali kunena kuti, ‘Angadziwe ndani, mwina Yehova angandikomere mtima ndipo mwanayu angakhale ndi moyo?’+ 23 Koma tsopano popeza wamwalira, ndisale kudya chifukwa chiyani? Kodi ndingamuukitse?+ Inenso tsiku lina ndidzamwalira,+ koma iyeyo sangabwerere kwa ine.”+

24 Ndiyeno Davide anayamba kutonthoza mkazi wake Bati-seba.+ Kuwonjezera apo, analowa kwa iye ndipo anagona naye. Patapita nthawi, anamuberekera mwana wamwamuna+ amene anamutcha dzina lakuti Solomo.*+ Yehova anam’konda mwana ameneyu.+ 25 Chotero Mulungu anatuma Natani+ mneneri kuti mwanayo akamutche dzina lakuti Yedediya,* chifukwa Yehova anam’konda.*

26 Ndiyeno Yowabu+ anapitiriza kumenyana ndi mzinda wa Raba+ wa ana a Amoni, ndipo analanda mzinda wachifumu. 27 Choncho Yowabu anatumiza mithenga kwa Davide kuti: “Ndamenyana ndi mzinda wa Raba.+ Ndalandanso mzinda wa madzi.* 28 Tsopano sonkhanitsani anthu otsalawo kuti muuthire nkhondo mzindawu ndi kuulanda, kuti ndisaulande ndine, kuopera kuti lingatchuke ndi dzina langa.”

29 Choncho Davide anasonkhanitsa anthu onse ndi kupita ku Raba kumene anathira nkhondo mzindawo ndi kuulanda. 30 Iye analanda chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,*+ ndipo anthu anaveka Davide chisoticho. Golide wa chisoticho anali wolemera talente limodzi,* ndipo chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Zinthu zimene anafunkha+ mumzindawo zinali zochuluka kwambiri. 31 Davide anatulutsa anthu amene anali mumzindawo kuti akawagwiritse ntchito yocheka miyala, kusula zitsulo zakuthwa,+ nkhwangwa zachitsulo ndi kuumba njerwa. Zimenezi n’zimene anachitira mizinda yonse ya ana a Amoni. Pamapeto pake, Davide pamodzi ndi anthu onse anabwerera ku Yerusalemu.

13 Pambuyo pa zinthu zimenezi, zinachitika kuti, Abisalomu+ mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola dzina lake Tamara.+ Ndipo Aminoni+ mwana wa Davide anayamba kukonda kwambiri+ Tamara. 2 Zimenezi zinam’vutitsa maganizo kwambiri Aminoni, moti anadwala+ chifukwa cha mlongo wake Tamara. Popeza Tamara anali namwali, zinali zovuta kwambiri+ kwa Aminoni kuti achite naye kalikonse.+ 3 Tsopano Aminoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu,+ mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide. Yehonadabu anali munthu wanzeru kwambiri. 4 Ndiyeno Yehonadabu anafunsa Aminoni kuti: “N’chifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu tsiku ndi tsiku umaoneka wosasangalala? Kodi sungandiuze?”+ Pamenepo Aminoni anamuuza kuti: “Ine ndikukonda kwambiri+ Tamara, mlongo+ wa m’bale wanga Abisalomu.” 5 Atatero, Yehonadabu anamuuza kuti: “Ugone pabedi lako ndi kunamizira kudwala.+ Mosakayikira bambo ako adzabwera kudzakuona, ndipo udzawauze kuti, ‘Chonde lolani kuti mlongo wanga Tamara abwere adzandipatse chakudya monga munthu wodwala. Ndikufuna kuti andipangire chakudya chonditonthoza pamaso panga, ine ndikuona, ndipo ndidye kuchokera m’manja mwake.’”+

6 Pamenepo Aminoni anagona pansi ndi kunamizira kudwala.+ Zitatero mfumu inabwera kudzamuona ndipo Aminoni anauza mfumuyo kuti: “Chonde, lolani kuti mlongo wanga Tamara abwere adzandiphikire makeke pamaso panga, kuti ndidye chakudya kuchokera m’manja mwake monga wodwala.” 7 Zitatero, Davide anatumiza uthenga kwa Tamara amene anali kunyumba ndi kumuuza kuti: “Chonde, pita kunyumba ya Aminoni m’bale wako ukamupangire chakudya chomutonthoza.” 8 Choncho Tamara anapita kunyumba ya Aminoni+ m’bale wake, Aminoniyo atagona. Ndiyeno anatenga ufa ndi kuukanda ndipo kenako anaumba makeke* pamaso pa Aminoni ndi kuwaphika. 9 Pomalizira, anatenga chiwaya ndi kukhuthula makekewo Aminoni akuona. Koma Aminoni anakana kudya ndipo anati: “Uzani aliyense atuluke!”+ Pamenepo aliyense anatuluka.

10 Ndiyeno Aminoni anauza Tamara kuti: “Bweretsa chakudya chonditonthoza kuchipinda chogona kuti ndidye kuchokera m’manja mwako monga wodwala.” Pamenepo Tamara anatenga makeke amene anapangawo ndi kupita nawo kwa Aminoni m’bale wake m’chipinda chogona. 11 Atamuyandikira kuti adye, Aminoni anamugwira+ ndi kumuuza kuti: “Gona ndi ine+ mlongo wanga.”+ 12 Koma Tamara anamuuza kuti: “Ayi, m’bale wanga! Usandichititse manyazi,+ chifukwa zimenezi n’zachilendo mu Isiraeli.+ Usachite chinthu chopusa, chochititsa manyazi ngati chimenechi.+ 13 Ndipo ine nditani ndi chitonzo chimenechi? Komanso iwe ukhala ngati mmodzi mwa amuna opusa mu Isiraeli. Chonde lankhula ndi mfumu, pakuti sangakuletse kuti unditenge.” 14 Koma Aminoni sanamvere mawu ake. Popeza anali ndi mphamvu zoposa Tamara, anamuchititsa manyazi+ mwa kugona naye.+ 15 Aminoni atachita zimenezo anayamba kudana naye kwambiri. Anadana naye kwambiri kuposa mmene ankamukondera, moti Aminoni anamuuza kuti: “Nyamuka, choka muno!” 16 Pamenepo Tamara anati: “Ayi usatero m’bale wanga. Pakuti kundithamangitsa kumene ukuchitaku n’koipa kwambiri kuposa zimene wandichitazi!” Koma Aminoni sanamvere zimenezo.

17 Pamenepo Aminoni anaitana mtumiki wake womupatsira chakudya n’kumuuza kuti: “Chotsa munthu ameneyu pamaso panga ndi kupita naye panja, ndipo ukhome chitseko akatuluka.” 18 (Tamara anali atavala malaya amizeremizere,+ pakuti umu ndi mmene ana aakazi a mfumu amene anali anamwali anali kuvalira. Iwo anali kuvala malaya akunja odula manja amizeremizere.) Choncho mtumiki wake uja anamutenga ndi kupita naye panja, ndipo atamutulutsa anakhoma chitseko. 19 Kenako Tamara anadzithira phulusa+ kumutu ndi kung’amba malaya ake amizeremizere aja. Ndiyeno anaika manja ake pamutu+ n’kunyamuka kumapita, akulira.

20 Zitatero, m’bale wake Abisalomu+ anamuuza kuti: “Kodi si m’bale wako Aminoni+ amene wakuchitira choipa chimenechi? Tsopano khala chete mlongo wanga. Iyeyo ndi m’bale wako.+ Usadandaule ndi nkhani imeneyi.” Ndiyeno Tamara anayamba kukhala kunyumba ya m’bale wake Abisalomu ndipo sanali kucheza ndi wina aliyense. 21 Tsopano Mfumu Davide anamva zonse zimene zinachitika+ ndipo anakwiya kwambiri.+ 22 Abisalomu sanalankhule chilichonse, chabwino kapena choipa kwa m’bale wake Aminoni, pakuti Abisalomu anadana+ ndi Aminoni chifukwa chochititsa manyazi Tamara mlongo wake.

23 Patapita zaka ziwiri zathunthu, anthu ena anali kumeta ubweya wa nkhosa+ za Abisalomu ku Baala-hazori, pafupi ndi Efuraimu.+ Choncho Abisalomu anaitanira ana onse aamuna a mfumu kumeneko.+ 24 Ndiyeno Abisalomu anapita kwa mfumu ndi kunena kuti: “Ine mtumiki wanu ndili ndi anthu amene akumeta ubweya wa nkhosa! Chonde, ndikupempha kuti inu mfumu ndi atumiki anu mupite pamodzi ndi ine mtumiki wanu.” 25 Koma mfumu inayankha Abisalomu kuti: “Ayi mwana wanga. Tisachite kupita tonse, chifukwa tingakhale mtolo wolemetsa kwa iwe.” Ngakhale kuti Abisalomu anachondererabe,+ mfumu sinalole kupita koma inamudalitsa.+ 26 Pamapeto pake Abisalomu anati: “Ngati inuyo simubwera, chonde lolani kuti Aminoni m’bale wanga apite nafe.”+ Pamenepo mfumu inamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukufuna kuti apite nawe?” 27 Ndiyeno Abisalomu anayamba kumuchonderera,+ moti mfumu inalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye.

28 Kenako Abisalomu analamula omutumikira kuti: “Muonetsetse chonde kuti Aminoni akangosangalala mumtima mwake ndi vinyo,+ ine n’kukuuzani kuti, ‘Mukantheni Aminoni!’ pamenepo mumuphe. Musaope.+ Kodi si ndine amene ndakulamulani? Chitani zinthu mwamphamvu ndipo khalani olimba mtima.” 29 Pamenepo atumiki a Abisalomu anachitira Aminoni monga mmene Abisalomuyo anawalamulira.+ Zitatero, ana onse a mfumu ananyamuka ndipo aliyense anakwera nyulu* yake ndi kuthawa. 30 Kenako ana amenewa ali m’njira, uthenga unafika kwa Davide kuti: “Abisalomu wapha ana onse a mfumu ndipo palibe amene watsala.” 31 Mfumu itamva zimenezi inaimirira ndi kung’amba zovala zake+ n’kugona pansi.+ Atumiki ake onse anaimirira pafupi ndi mfumuyo atang’ambanso zovala zawo.+

32 Koma Yehonadabu+ mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide anati: “Inu mbuyanga musaganize kuti ndi ana onse a mfumu amene aphedwa, pakuti ndi Aminoni yekha amene wafa.+ Abisalomu ndi amene walamula zimenezi kuti zichitike pakuti anakonzeratu+ zimenezi kuyambira pa tsiku limene Aminoniyo anachititsa manyazi+ Tamara mlongo wake.+ 33 Tsopano mbuyanga mfumu, musavutike mtima ndi mawu amenewa onena kuti, ‘Ana onse a mfumu afa,’ pakuti ndi Aminoni yekha amene wafa.”

34 Panthawiyi n’kuti Abisalomu atathawa.+ Pambuyo pake mnyamata wina amene anali mlonda,+ anakweza maso ndipo anaona anthu ambiri akubwera kumbuyo kwake mumsewu umene unali m’mphepete mwa phiri. 35 Pamenepo Yehonadabu+ anauza mfumu kuti: “Taonani! Ana a mfumu akubwera. Zachitika monga mwa mawu a mtumiki wanu.”+ 36 Ndiyeno atangomaliza kulankhula, ana a mfumu aja anafika ndipo anayamba kulira mokweza mawu. Mfumu nayonso pamodzi ndi atumiki ake onse analira kwadzaoneni. 37 Koma Abisalomu anathawa ndi kupita kwa Talimai,+ mfumu ya dziko la Gesuri,+ amene anali mwana wamwamuna wa Amihudi. Davide anali kulira+ tsiku ndi tsiku chifukwa cha imfa ya Aminoni mwana wake. 38 Chotero Abisalomu anathawa ndi kupita ku Gesuri+ ndipo anakhala kumeneko zaka zitatu.

39 Pamapeto pake mfumu Davide inalakalaka kupita kwa Abisalomu, pakuti anali atadzitonthoza pambuyo pa imfa ya Aminoni.

14 Tsopano Yowabu,+ mwana wa Zeruya+ anadziwa kuti mtima wa mfumu ukulakalaka Abisalomu.+ 2 Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mkazi wanzeru.+ Atabwera naye, Yowabu anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene ali panyengo yolira maliro, ndipo uvale zovala za panyengo yolira maliro, komanso usadzole mafuta.+ Ukatero ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa masiku ambiri.+ 3 Ndiyeno upite kuti ukaonekere kwa mfumu ndipo ukalankhule nayo mawu awa.” Atatero, Yowabu anamuuza zokanena.+

4 Pamenepo mkazi wa ku Tekowa uja anapita kukaonana ndi mfumu, ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ kenako anadzigwetsa pansi, n’kunena kuti: “Chonde mfumu, ndipulumutseni!”+ 5 Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Kodi chavuta ndi chiyani?” Mkaziyo anayankha kuti: “Ine ndine mkazi wamasiye,+ pakuti mwamuna wanga anamwalira. 6 Ndiyeno ine mtumiki wanu ndinali ndi ana awiri aamuna. Tsiku lina anawo anayamba kulimbana ali kuthengo+ kopanda munthu wowaleretsa.+ Pamapeto pake wina anakantha mnzake ndi kumupha. 7 Tsopano banja lonse landiukira ine mtumiki wanu ndipo aliyense akunena kuti, ‘Bweretsa wopha m’bale wakeyo+ kuti timuphe chifukwa cha moyo wa m’bale wake amene anamupha,+ ndipo tiwononge wolandira cholowayo!’ Tsopano anthuwa adzazimitsa makala anga onyeka otsalawo, kuti pasakhale wosunga dzina la mwamuna wanga kapena mbewu yake yotsala padziko lapansi.”+

8 Ndiyeno mfumu inauza mkaziyo kuti: “Pita kunyumba kwako ndipo ine ndisamalira nkhani imeneyi.”+ 9 Pamenepo mkazi wa ku Tekowayo anauza mfumu kuti: “Mbuyanga mfumu, kulakwa kukhale kwanga ndi kwa nyumba ya bambo anga,+ koma mfumu ndi mpando wake wachifumu ndi zosalakwa.” 10 Mfumu inapitiriza kunena kuti: “Ngati aliyense angakufunse nkhani imeneyi, ubwere naye kwa ine ndipo sadzakuzunzanso.” 11 Koma mkaziyo anati: “Chonde mfumu, kumbukirani Yehova Mulungu wanu+ kuti munthu wobwezera magazi+ asapitirize kuwononga, ndi kuti anthu amenewa asaphe mwana wanga.” Pamenepo mfumu inati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi+ la mwana wako silidzagwa pansi.” 12 Ndiyeno mkaziyo anati: “Ndiloleni ine mtumiki wanu,+ chonde, ndilankhule mawu amodzi+ kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumu inamuuza kuti: “Lankhula!”+

13 Ndiyeno mkaziyo anapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chiyani inu mfumu mwachitira+ anthu a Mulungu+ zinthu zowawononga? Popeza inu mfumu munapitikitsa+ mwana wanu, ndipo mwalephera kumuitanitsa, muli ndi mlandu+ pa zimene mwafotokozazi. 14 Tonsefe tidzafa+ ndi kukhala ngati madzi otayika amene sawoleka. Koma Mulungu wakonza zinthu+ ndipo ali ndi zifukwa zothandiza kuti munthu wopitikitsidwa asapitirize kukhala wopitikitsidwa. 15 Chifukwa chakuti anthu andichititsa mantha, ndabwera kudzalankhula mawu amenewa ndi inu mbuyanga mfumu. N’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndinati, ‘Ndiloleni chonde ndilankhule nanu mfumu. Mwina mfumu idzachitapo kanthu pa mawu a kapolo wanu wamkazi. 16 Choncho, chifukwa chakuti mfumu yandimvera kuti indilanditse ine kapolo wake wamkazi m’manja mwa munthu wofuna kuwononga ine ndi mwana wanga wamwamuna yekhayo, kutichotsa pa cholowa chathu choperekedwa ndi Mulungu,’+ 17 ine mtumiki wanu ndinaganiza kuti, ‘Mawu a mbuyanga mfumu andipatsa mpumulo.’ Pakuti inu mbuyanga mfumu muli ngati mngelo+ wa Mulungu woona, wokhoza kusiyanitsa chabwino ndi choipa.+ Ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.”

18 Tsopano mfumu inayankha mkaziyo kuti: “Usandibisire kalikonse pa zimene ndikufuna kukufunsa.”+ Pamenepo mkaziyo ananena kuti: “Lankhulani mbuyanga mfumu.” 19 Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Kodi Yowabu+ ndi amene wakutuma?”+ Pamenepo mkaziyo anayankha kuti: “Pali moyo wanu+ mbuyanga mfumu, palibe munthu angapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa zonse zimene inu mbuyanga mfumu mwanena. Mtumiki wanu Yowabu ndi amene wandituma ndi kundiuza zonse zimene ndalankhula nanu.+ 20 Mtumiki wanu Yowabu wachita zimenezi kuti asinthe mmene mukuonera nkhaniyi. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru ngati mngelo+ wa Mulungu woona, moti mukudziwa zonse za padziko lapansi.”

21 Zitatero, mfumu inauza Yowabu kuti: “Chabwino, ndichita zimene wanena.+ Choncho pita ukatenge mnyamatayo Abisalomu ndipo ubwere naye.”+ 22 Yowabu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kudalitsa mfumu,+ n’kunena kuti: “Lero ndadziwa kuti ine mtumiki wanu mwandikomera mtima,+ mbuyanga mfumu, chifukwa chakuti inu mfumu mwamvera mawu anga ine mtumiki wanu.” 23 Yowabu atanena mawu amenewa ananyamuka ndi kupita ku Gesuri,+ ndipo anabweretsa Abisalomu ku Yerusalemu.+ 24 Koma mfumu inanena kuti: “Apite kunyumba kwake, koma asaone nkhope yanga.”+ Choncho Abisalomu anatembenukira kunyumba kwake, ndipo sanaonane ndi mfumu.

25 Tsopano mu Isiraeli yense munalibe mwamuna wina wotamandika kwambiri koposa Abisalomu chifukwa cha kukongola kwake.+ Iye analibe chilema chilichonse kuyambira kuphazi mpaka paliwombo. 26 Abisalomu anali kumeta tsitsi lake kumapeto kwa chaka chilichonse chifukwa linali kumulemera kwambiri.+ Ndipo akameta tsitsi lakelo, anali kuliyeza kulemera kwake ndipo linali kukwana masekeli* 200 poliyeza ndi mwala wachifumu woyezera kulemera kwa zinthu.* 27 Abisalomu anabereka ana aamuna atatu+ ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Ameneyu anali chiphadzuwa chadzaoneni.+

28 Abisalomu anapitiriza kukhala m’Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, ndipo sanaonane ndi mfumu.+ 29 Zitatero, Abisalomu anaitanitsa Yowabu kuti amutume kwa mfumu, koma Yowabu sanalole kupita kwa Abisalomu. Iye anamuitanitsanso kachiwiri, koma sanalole kuti apite kwa Abisalomu. 30 Pamapeto pake, Abisalomu anauza atumiki ake kuti: “Pafupi ndi munda wanga pali munda wa Yowabu umene uli ndi balere. Mupite kumeneko ndipo mukautenthe ndi moto.”+ Choncho atumiki a Abisalomu anatentha mundawo ndi moto.+ 31 Pamenepo Yowabu ananyamuka n’kupita kunyumba kwa Abisalomu. Atafika kumeneko anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani atumiki ako anatentha munda wanga?” 32 Abisalomu anayankha kuti: “Ine ndinakutumizira uthenga wonena kuti, ‘Ubwere kuno ndikutume kwa mfumu ukaiuze kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabwerako ku Gesuri?+ Zikanakhala bwino ndikanangokhalabe komweko. Tsopano ndikufuna ndionane ndi mfumu, ndipo ngati ndili wolakwa,+ mfumu indiphe.”’”

33 Chotero Yowabu anapita kukaonana ndi mfumu ndipo anaiuza mawu amenewa. Ndiyeno mfumu inaitanitsa Abisalomu, moti iye anabwera kudzaonana ndi mfumu. Abisalomu atafika anagwada ndi kuwerama, kenako anadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Zitatero, mfumu inapsompsona Abisalomu.+

15 Ndiyeno pambuyo pa zinthu zimenezi, Abisalomu anadzipangira galeta lokokedwa ndi mahatchi, ndipo amuna 50 anali kuthamanga patsogolo pake.+ 2 Tsopano Abisalomu anadzuka m’mawa kwambiri+ ndi kukaima pambali pa msewu wa kuchipata.+ Ndiyeno munthu aliyense amene anali ndi mlandu akafika kuti mlandu wake ukaweruzidwe ndi mfumu,+ Abisalomu anali kumuitana ndi kumuuza kuti: “Wachokera mumzinda uti?” Poyankha munthuyo anali kunena kuti: “Ine mtumiki wanu ndachokera mu limodzi la mafuko a Isiraeli.” 3 Pamenepo Abisalomu anali kumuuza kuti: “Taona, nkhani yakoyi ili bwino ndipo ndi yosavuta. Koma mfumu ilibe aliyense woti amvetsere nkhani yakoyi.”+ 4 Ndiyeno Abisalomu anali kupitiriza kunena kuti: “Haa! Zikanakhalatu bwino ndikanaikidwa kukhala woweruza m’dziko lino+ kuti munthu aliyense wokhala ndi mlandu kapena wofuna chiweruzo azibwera kwa ine, ndipo ndikanamuchitira chilungamo.”+

5 Ndiyeno zimene zinali kuchitikanso n’zakuti, munthu akafika pafupi kuti amuweramire, Abisalomu anali kutambasula dzanja lake ndi kumugwira+ kenako n’kumupsompsona. 6 Abisalomu anapitiriza kuchita zinthu zoterezi kwa Aisiraeli onse amene anali kubwera kwa mfumu kuti iwaweruzire milandu yawo, moti Abisalomu anapitiriza kukopa mitima ya anthu a mu Isiraeli.+

7 Tsopano kumapeto kwa zaka 40,* Abisalomu anauza mfumu kuti: “Chonde, ndiloleni ndichoke, ndipite ku Heburoni+ kukakwaniritsa lonjezo langa lalikulu limene ndinalonjeza Yehova.+ 8 Pakuti ine mtumiki wanu ndinalonjeza lonjezo lalikulu+ pamene ndinali kukhala ku Gesuri,+ ku Siriya, ndipo ndinati, ‘Yehova akandilola kubwerera ku Yerusalemu, ndiyenera kupereka nsembe kwa Yehova.’”+ 9 Pamenepo mfumu inamuyankha kuti: “Pita mu mtendere.”+ Zitatero, ananyamuka ndi kupita ku Heburoni.

10 Ndiyeno Abisalomu anatumiza akazitape+ m’mafuko onse a Isiraeli ndipo anawauza kuti: “Mukangomva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, munene kuti, ‘Abisalomu wakhala mfumu+ ku Heburoni!’”+ 11 Pochoka, Abisalomu anatenga anthu 200 mu Yerusalemu. Amenewa anawaitana ndipo ananyamuka m’chimbulimbuli+ osadziwa kena kalikonse. 12 Kuwonjezera apo, pamene Abisalomu anali kupereka nsembe, anaitanitsa Ahitofeli+ Mgilo,+ phungu wa Davide,+ kuchoka kumzinda wakwawo wa Gilo.+ Chiwembu+ chimenecho chinapitiriza kukula ndipo chiwerengero cha anthu amene anali kutsatira Abisalomu chinapitiriza kuwonjezeka.+

13 Patapita nthawi, munthu wina anauza Davide kuti: “Mitima+ ya anthu a mu Isiraeli yatsatira Abisalomu.” 14 Nthawi yomweyo, Davide anauza atumiki ake onse amene anali naye limodzi mu Yerusalemu, kuti: “Nyamukani, tiyeni tithawe,+ pakuti sipapezeka munthu wopulumuka m’manja mwa Abisalomu. Chitani changu, pakuti mwina angafike mofulumira ndi kutipeza n’kutichitira choipa komanso kukantha mzinda ndi lupanga!”+ 15 Pamenepo atumiki a mfumu anauza mfumu kuti: “Ife atumiki anu tichita mogwirizana ndi zimene inu mbuyathu mfumu mwasankha.”+ 16 Choncho mfumu inanyamuka ndi kutuluka ndipo anthu onse a m’nyumba yake anaitsatira.+ Koma mfumuyo inasiya akazi 10, amene anali adzakazi ake,+ kuti asamalire nyumba. 17 Mfumu inatulukadi ndi kupitiriza ulendo wake pamodzi ndi anthu onse amene anali kuitsatira ndipo anaima ku Beti-merehaki.*

18 Kumeneko atumiki onse a mfumu, Akereti onse ndi Apeleti+ onse, anali kudutsa pamaso pake. Komanso Agiti+ onse, amuna 600 amene anamutsatira* kuchokera ku Gati+ anali kudutsa pamaso pake. 19 Kenako mfumu inauza Itai+ Mgiti kuti: “Kodi iweyo ukupita nafe chifukwa chiyani? Bwerera+ ukakhale ndi mfumu, pakuti ndiwe mlendo komanso ndiwe wothawa kwanu. 20 Iwe wabwera dzulo lomweli, kodi lero uyende+ ndi ife kupita kulikonse kumene ine ndikupita? Bwerera, tenga abale ako ndi kubwerera nawo limodzi, ndipo Yehova akusonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi kukhulupirika kwake!”+ 21 Koma Itai anayankha mfumu kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo, komanso pali moyo wanu mbuyanga mfumu,+ kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzapita ine mtumiki wanu ndidzapitanso komweko, ndipo ndili wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”+ 22 Pamenepo Davide anauza Itai+ kuti: “Dutsa, upite.” Choncho Itai Mgiti anadutsa pamaso pake komanso amuna onse amene anali kuyenda naye ndi ana onse amene anali naye.

23 Anthu onse a m’dzikoli anali kulira mokweza mawu,+ ndipo anthu onse amene anali ndi Davide anali kudutsa pamaso pake. Mfumu inaimirira pafupi ndi chigwa* cha Kidironi,+ ndipo anthu onse anali kudutsa mumsewu waukulu wopita kuchipululu. 24 Kumeneko kunalinso Zadoki+ pamodzi ndi Alevi+ onse atanyamula+ likasa+ la pangano la Mulungu woona. Choncho Aleviwo anatula pansi likasa la Mulungu woona pafupi ndi Abiyatara+ kufikira anthu onse atamaliza kudutsa kuchokera mumzinda. 25 Ndiyeno mfumu inauza Zadoki kuti: “Tenga likasa+ la Mulungu woona ndi kubwerera nalo mumzinda.+ Yehova akandikomera mtima adzandibwezeretsa mumzinda ndipo ndidzaliona. Ndidzaonanso malo amene limakhala.+ 26 Koma akanena kuti, ‘Sindikusangalala nawe,’ ine ndidzavomereza zilizonse zimene adzandichitira.”+ 27 Pamenepo mfumu inapitiriza kuuza Zadoki wansembe kuti: “Iwe ndi wamasomphenya,*+ si choncho kodi? Bwerera kumzinda mu mtendere. Bwerera pamodzi ndi Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. Mubwerere ndi ana anu awiri amene muli nawowa. 28 Taona, ine ndikhalabe pamalo owolokera amene ali pafupi ndi chipululu kufikira amuna inu mutatumiza uthenga wondidziwitsa mmene zinthu zilili.”+ 29 Choncho Zadoki ndi Abiyatara anatenga likasa la Mulungu woona ndi kubwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anapitiriza kukhala kumeneko.

30 Davide anali kukwezeka zitunda za phiri la Maolivi+ akulira, ataphimba kumutu kwake.+ Anali kuyenda wosavala nsapato ndipo aliyense mwa anthu amene anali naye anaphimba kumutu kwake ndipo onse anali kuyenda akulira.+ 31 Kenako uthenga unafika kwa Davide wonena kuti: “Ahitofeli nayenso ali pakati pa anthu amene akukonza chiwembu+ pamodzi ndi Abisalomu.”+ Pamenepo Davide anati:+ “Inu Yehova!+ Chonde, sandutsani malangizo a Ahitofeli kuti akhale opusa.”+

32 Ndiyeno pamene Davide anafika pamwamba pa phiri pamene anthu anali kugwadira Mulungu, anaona Husai+ Mwareki+ akubwera kudzakumana naye, atang’amba chovala chake ndiponso atadzithira dothi kumutu.+ 33 Pamenepo Davide anamuuza kuti: “Ukapita nane limodzi, ukhala mtolo wolemetsa kwa ine.+ 34 Koma ukabwerera kumzinda ndi kukauza Abisalomu kuti, ‘Inu Mfumu ine ndine mtumiki wanu. Kale ndinali mtumiki wa bambo anu, koma tsopano ndine mtumiki wanu,’+ pamenepo ukanditsutsire+ malangizo a Ahitofeli. 35 Kodi kumeneko suli ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembe?+ Chilichonse chimene ukamve kuchokera kunyumba ya mfumu ukauze Zadoki ndi Abiyatara ansembe.+ 36 Taona, iwo ali ndi ana amuna awiri, Ahimazi+ mwana wa Zadoki ndi Yonatani+ mwana wa Abiyatara. Choncho amuna inu mukatume amenewa kuti adzandiuze zonse zimene mungamve.” 37 Pamenepo Husai, mnzake wa Davide,+ anabwerera kumzinda. Ndipo Abisalomu+ anabwera ku Yerusalemu.

16 Davide atapitirira pang’ono pamwamba pa phiri paja,+ anaona Ziba+ mtumiki wa Mefiboseti+ akubwera kudzakumana naye. Iye anali ndi abulu awiri+ okhala ndi zishalo ndipo abuluwa anali atanyamula mitanda 200 ya mkate,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100,+ zipatso za m’chilimwe* 100+ zouma zoumba pamodzi ndiponso mtsuko waukulu wa vinyo.+ 2 Ndiyeno mfumu inafunsa Ziba kuti: “Kodi zinthu zimene watengazi n’zachiyani?”+ Poyankha Ziba anati: “Abuluwa ndatengera anthu a m’nyumba ya mfumu kuti azikwerapo, mkate ndi makeke a zipatso za m’chilimwe ndatengera anyamata+ kuti adye, ndipo vinyo ndatengera munthu wotopa+ m’chipululu+ kuti amwe.” 3 Tsopano mfumu inafunsa kuti: “Kodi mwana wa mbuye wako ali kuti?”+ Pamenepo Ziba anauza mfumu kuti: “Watsalira ku Yerusalemu, pakuti wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+ 4 Kenako mfumu inauza Ziba kuti: “Taona, zonse zimene zinali za Mefiboseti+ ndi zako.” Pamenepo Ziba anati: “Ndikuwerama+ pamaso panu. Pitirizani kundikomera mtima mbuyanga mfumu.”

5 Ndiyeno Mfumu Davide inafika ku Bahurimu.+ Kumeneko inaona mwamuna wina wa m’banja la Sauli, dzina lake Simeyi,+ mwana wa Gera akutuluka ndipo anali kulankhula mawu onyoza.+ 6 Iye anayamba kuponya miyala Davide ndi atumiki onse a Mfumu Davide. Anthu onse ndi amuna onse amphamvu anali kudzanja lamanja ndi lamanzere la mfumu. 7 Ponyoza, Simeyi anali kunena kuti: “Choka, choka, munthu wa mlandu wamagazi+ ndi wopanda pake iwe!+ 8 Yehova wakubwezera mlandu wonse wa magazi a nyumba ya Sauli amene iwe unamulowa m’malo monga mfumu. Yehova wapereka ufumu m’manja mwa Abisalomu mwana wako. Ndipo tsopano tsoka lakugwera chifukwa uli ndi mlandu wamagazi!”+

9 Pamapeto pake Abisai mwana wa Zeruya+ anauza mfumu kuti: “N’chifukwa chiyani galu wakufa uyu+ akukunyozani mbuyanga mfumu?+ Ndiloleni ndipite chonde ndikam’dule mutu.”+ 10 Koma mfumu inati: “Ndili nanu chiyani+ inu ana a Zeruya?+ Musiyeni anyoze+ chifukwa Yehova wamuuza kuti,+ ‘Munyoze Davide!’ Choncho ndani angamufunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani iwe wachita zimenezi?’”+ 11 Ndiyeno Davide anapitiriza kuuza Abisai ndi atumiki ake onse kuti: “Ngati mwana wanga weniweni, wotuluka m’chiuno mwanga akufunafuna moyo wanga,+ kuli bwanji M’benjamini uyu!+ Musiyeni anyoze, pakuti Yehova wamuuza kuti atero! 12 Mwina Yehova aona+ ndi diso lake, ndipo lero Yehova abwezeretsa kwa ine zinthu zabwino m’malo mwa temberero la Simeyi.”+ 13 Pamenepo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anapitiriza kuyenda mumsewu. Simeyi anali kuyenda m’mbali mwa phiri pafupi ndi Davide ndipo anali kuyenda akulankhula mawu onyoza.+ Iye analinso kuponya miyala akuyenda m’mbali mwa phirimo pafupi ndi Davide ndiponso anali kuwaza fumbi lambiri.+

14 Patapita nthawi, mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika kumene anali kupita ali otopa. Choncho iwo anaima kuti apume.+

15 Koma Abisalomu ndi anthu onse, amuna a Isiraeli, analowa mu Yerusalemu+ ndipo Ahitofeli+ anali naye limodzi. 16 Ndiyeno Husai+ Mwareki,+ mnzake wa Davide,+ atangofika kwa Abisalomu anauza Abisalomu kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!+ Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” 17 Pamenepo Abisalomu anauza Husai kuti: “Kodi kumeneku ndiko umati kusonyeza mnzako kukoma mtima kosatha? N’chifukwa chiyani sunapite ndi mnzako?”+ 18 Poyankha Husai anauza Abisalomu kuti: “Iyayi, amene Yehova wamusankha komanso amene anthu awa ndi anthu onse a mu Isiraeli amusankha, ine ndidzakhala wake ndipo ndidzakhala ndi iye. 19 Ndibwereze kunena kuti, Ine ndingatumikire ndani? Kodi sindiyenera kutumikira mwana wake? Monga mmene ndinatumikira bambo anu, ndichitanso chimodzimodzi kwa inu.”+

20 Kenako Abisalomu anafunsa Ahitofeli kuti: “Amuna inu, nenani maganizo anu.+ Tichite chiyani?” 21 Pamenepo Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ugone ndi adzakazi a bambo ako+ amene wawasiya kuti azisamalira nyumba.+ Ukatero Aisiraeli onse adzamva kuti wadzinunkhitsa+ pamaso pa bambo ako,+ ndipo manja+ a anthu onse amene ali ndi iwe adzalimba ndithu.” 22 Choncho anamangira Abisalomu hema padenga,+ ndipo Abisalomu anayamba kugona ndi adzakazi a bambo ake,+ Aisiraeli onse akuona.+

23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe.

17 Ndiyeno Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ndilole chonde, ndisankhe amuna 12,000 kuti ndithamangitse Davide lero usiku.+ 2 Ndimupeza ali wotopa ndi wofooka manja ake onse,+ ndipo adzanjenjemera ndithu chifukwa cha ine. Pamenepo anthu onse amene ali naye adzathawa, ndipo ine ndidzapha mfumu ili yokha.+ 3 Ndilole ndibweretse anthu onse kwa iwe. Pakuti kubwerera kwa anthu onse kukudalira zimene zingachitikire munthu amene ukumusakasakayu, ndipo anthu onse adzakhala mu mtendere.” 4 Mawu amenewa anali abwino kwa Abisalomu+ ndi kwa akulu onse a Isiraeli.

5 Koma Abisalomu anati: “Kaitanenso Husai+ Mwareki kuti timve maganizo ake.” 6 Choncho Husai anabwera kwa Abisalomu. Ndiyeno Abisalomu anamuuza kuti: “Mawu amenewa ndi amene Ahitofeli wanena. Kodi tichite zimene wanenazi? Ngati unena kuti ayi, iweyo tiuze zochita.” 7 Pamenepo Husai anauza Abisalomu kuti: “Malangizo amene Ahitofeli wapereka ulendo uno sali bwino ayi!”+

8 Ndiyeno Husai anapitiriza kunena kuti: “Iwe ukuwadziwa bwino bambo wako ndi amuna amene ali nawo kuti iwo ndi amphamvu+ ndipo mitima ikuwapweteka+ ngati chimbalangondo chimene chataya ana ake kuthengo.+ Ukudziwanso bwino kuti bambo wako ndi munthu wankhondo+ ndipo sangagone kumene kuli anthu. 9 Ndipotu panopa akubisala+ m’dzenje linalake kapena m’malo ena. Ndiyeno iyeyo akakhala woyamba kuukira anthu, nkhani idzafala kuti, ‘Anthu amene akutsatira Abisalomu agonjetsedwa!’ 10 Choncho ngakhale mwamuna wolimba mtima amene ali ndi mtima ngati wa mkango+ adzafooka+ ndithu. Izi zili choncho chifukwa Isiraeli yense akudziwa kuti bambo wako ndi mwamuna wamphamvu,+ ngatinso mmene alili amuna olimba mtima amene ali naye.+ 11 Ndiye ine malangizo anga ndi onena kuti: Sonkhanitsa ndithu Isiraeli yense pamaso pako kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Akhale ochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,+ ndipo iweyo uwatsogolere kunkhondo.+ 12 Ukatero, tikamuukire kumene tikudziwa kuti tikhoza kum’peza,+ ndipo tikam’fikira ngati mmene mame+ amagwera pansi. Pamenepo sipadzakhala aliyense wopulumuka, iyeyo ngakhale amuna onse amene ali naye. 13 Ngati angathawire mumzinda uliwonse, ife tidzapita ndi Isiraeli yense kukawononga mzinda umenewo ndi kuukokera kuchigwa* ndi zingwe. Mumzindawo simudzatsala ngakhale mwala wa nkhulungo.”+

14 Kenako Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli anati: “Malangizo a Husai Mwareki ndi abwino+ kusiyana ndi malangizo a Ahitofeli!” Ndipo Yehova anaonetsetsa+ kuti anthuwo asatsatire malangizo+ a Ahitofeli ngakhale kuti anali abwino.+ Yehova anachita zimenezi kuti adzetsere Abisalomu tsoka.+

15 Pambuyo pake Husai anauza Zadoki+ ndi Abiyatara ansembe, kuti: “Ahitofeli wapereka malangizo kwa Abisalomu ndi akulu a Isiraeli ndipo wanena zakutizakuti, koma malangizo amene ine ndapereka, ndanena zakutizakuti. 16 Ndipo tsopano tumizani uthenga mwamsanga kwa Davide+ wakuti, ‘Lero musagone m’chipululu, muwoloke ndithu+ kuopera kuti inu mfumu pamodzi ndi anthu onse amene muli nawo mungamezedwe.’”+

17 Pamene Yonatani+ ndi Ahimazi+ anali ataimirira pa Eni-rogeli,+ kapolo wamkazi anapita kumeneko ndi kuwauza zonse. Choncho iwo anachoka pakuti anafunika kukauza Mfumu Davide. Iwowa sanayese n’komwe kulowa mumzinda kuopera kuti angawazindikire. 18 Komabe mnyamata wina anawaona ndipo anapita kukauza Abisalomu. Choncho awiriwo anachoka mofulumira ndi kupita kunyumba ya munthu wina amene anali ndi chitsime pakhomo pake ku Bahurimu,+ ndipo iwo analowa m’chitsimemo. 19 Atalowa m’chitsimemo, mkazi wa munthuyo anatenga chotchingira ndi kuchiyala pachitsimepo, kenako anaunjikapo tirigu wosinja,+ ndipo palibe amene anadziwa chilichonse. 20 Tsopano atumiki a Abisalomu anafika kunyumba ya mkaziyo n’kunena kuti: “Kodi Ahimazi ndi Yonatani ali kuti?” Poyankha mkaziyo anawauza kuti: “Adutsa pano kulowera kumtsinje.”+ Pamenepo anapitiriza kuwafunafuna koma sanawapeze,+ choncho anabwerera ku Yerusalemu.

21 Ndiyeno atumiki a Abisalomu atachoka, Ahimazi ndi Yonatani anatuluka m’chitsimemo ndi kupita kukauza Mfumu Davide kuti: “Anthu inu nyamukani mwamsanga muwoloke mtsinje, pakuti Ahitofeli wapereka malangizo+ ndipo wanena zakutizakuti kuti athane nanu.” 22 Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, ndipo anawoloka Yorodano mpaka m’mawa.+ Onse anawoloka Yorodano popanda wotsala.

23 Koma Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanawagwiritse ntchito,+ anakwera bulu wake ndi kunyamuka kupita kunyumba yake kumzinda wakwawo.+ Kenako anakonzekeretsa banja lake+ ndipo anadzimangirira+ moti anafa.+ Chotero anaikidwa m’manda+ a makolo ake.

24 Davide anafika ku Mahanaimu+ ndipo Abisalomu nayenso anawoloka Yorodano pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli amene anali naye. 25 Ndiyeno Abisalomu anasankha Amasa+ kukhala mtsogoleri wagulu lankhondo kulowa m’malo mwa Yowabu.+ Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Itara,+ Mwisiraeli amene anagona ndi Abigayeli,+ mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wake wa Zeruya, mayi wake wa Yowabu. 26 Isiraeli ndi Abisalomu anamanga msasa m’dziko la Giliyadi.+

27 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Davide atangofika ku Mahanaimu, Sobi mwana wamwamuna wa Nahasi, wochokera ku Raba,+ mzinda wa ana a Amoni,+ komanso Makiri+ mwana wa Amiyeli,+ wochokera ku Lo-debara ndi Barizilai+ Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu,+ 28 anabweretsa makama, mabeseni, ziwiya zadothi, tirigu, balere, ufa,+ tirigu wokazinga,+ nyemba zikuluzikulu,+ mphodza+ ndi tirigu wowamba. 29 Iwo anabweretsanso uchi,+ mafuta a mkaka,+ wa ng’ombe ndiponso nkhosa. Anabweretsa zinthu zimenezi kuti Davide ndi anthu onse amene anali naye adye.+ Iwo anali kunena kuti: “Anthu amenewa ali ndi njala, atopa ndipo ali ndi ludzu m’chipululu.”+

18 Ndiyeno Davide anayamba kuwerenga anthu amene anali naye ndi kuwasankhira atsogoleri a magulu a anthu 1,000 ndi atsogoleri a magulu a anthu 100.+ 2 Atatero, Davide anagawa anthuwo m’magulu atatu.+ Gulu loyamba analipereka kwa Yowabu,+ gulu lachiwiri analipereka kwa Abisai+ mwana wa Zeruya, m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo gulu lachitatu analipereka kwa Itai+ Mgiti. Kenako mfumu inauza anthuwo kuti: “Inenso ndipita nanu sindilephera.” 3 Koma anthuwo anati: “Iyayi musapite,+ pakuti ngati titathawa kumeneko, sakasamala za ife.+ Ndipo ngati hafu ya ife tingafe, sakasamala za ife chifukwa inuyo ndinu wofunika kuposa anthu 10,000.+ Tsopano zingakhale bwino kuti muzititumikira ndi kutithandiza+ muli mumzinda mom’muno.” 4 Choncho mfumu inawauza kuti: “Ndichita zilizonse zimene inu mukuona kuti n’zabwino.”+ Pamenepo mfumu inangoima pambali pa chipata,+ ndipo anthu onse anapita kunkhondo m’magulu a anthu 100 ndi 1,000.+ 5 Ndiyeno mfumu inalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti: “Musachitire nkhanza+ mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ubwino wanga.” Anthu onse anamva zimene mfumu inalamula atsogoleri onsewa za nkhani yokhudza Abisalomu.

6 Ndiyeno anthu anapitiriza ulendo wawo wopita kuthengo kukakumana ndi Isiraeli. Kumeneko nkhondo inayambika m’nkhalango ya Efuraimu.+ 7 Pamapeto pake, anthu a Isiraeli+ anagonjetsedwa+ ndi atumiki a Davide, ndipo tsiku limenelo anthu ambiri anaphedwa, anthu 20,000. 8 Nkhondo imeneyi inafalikira dziko lonselo. Kuwonjezera apo, tsiku limenelo nkhalango inadya anthu ambiri kuposa amene anakanthidwa ndi lupanga.

9 Pamapeto pake, Abisalomu anakumana ndi atumiki a Davide. Abisalomu anali atakwera nyulu,* ndipo nyuluyo inadutsa paziyangoyango za nthambi za mtengo waukulu kwambiri. Choncho mutu wa Abisalomu unakola muziyangoyango za mtengo waukuluwo moti anali lendelende,+ koma nyulu imene anakwerapo ija inadutsa. 10 Ndiyeno munthu wina anaona zimenezo ndi kupita kukauza Yowabu kuti: “Ine ndaona Abisalomu ali lendelende+ mumtengo waukulu.” 11 Pamenepo Yowabu anafunsa munthu amene anali kumuuzayo kuti: “Tsopano iwe unamuona, nanga bwanji sunamuphe? Ukanamupha, unali udindo wanga kukupatsa ndalama 10 zasiliva ndi lamba.”+ 12 Koma munthuyo anauza Yowabu kuti: “Ngakhale ndikanalandira ndalama 1,000 zasiliva m’manja mwanga, sindikanatambasula dzanja langa ndi kupha mwana wa mfumu. Pakuti ife tinamva mfumu ikukulamulani inuyo, Abisai ndi Itai kuti, ‘Aliyense wa inu ateteze mnyamatayo Abisalomu.’+ 13 Apo ayi, ndikanachitira mfumu chinyengo, moti nkhani yonse sikanabisika kwa mfumu+ ndipo inu mukanandikanira.” 14 Pamenepo Yowabu anati: “Ndisachedwe chonchi ndi iwe!” Atatero anatenga mikondo itatu m’manja mwake ndi kulasa+ nayo mtima wa Abisalomu ali ndi moyo+ pakati pa mtengo waukulu. 15 Kenako atumiki 10 onyamula zida za Yowabu anafika pafupi ndi kukantha Abisalomu kuti afe.+ 16 Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ kuti anthu abwerere, kusiya kuthamangitsa Isiraeli. Chotero Yowabu analetsadi anthuwo. 17 Pamapeto pake anatenga Abisalomu ndi kum’ponya m’dzenje lalikulu m’nkhalangomo ndipo anamuunjikira mulu waukulu kwambiri wa miyala.+ Koma Aisiraeli onse, aliyense anathawira kunyumba yake.

18 Tsopano Abisalomu akali moyo anadzimangira chipilala.+ Chipilala chimenechi chili m’Chigwa cha Mfumu,+ pakuti iye anati: “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti asunge dzina langa monga chikumbukiro.”+ Choncho chipilala chimenecho anachitcha dzina lake+ ndipo chikudziwikabe ndi dzina lakuti Chipilala cha Abisalomu kufikira lero.

19 Ndiyeno Ahimazi+ mwana wa Zadoki anati: “Ndiloleni ndithamange ndikapereke uthenga kwa mfumu, chifukwa Yehova wamuweruza kuti amulanditse m’manja mwa adani ake.”+ 20 Koma Yowabu anamuuza kuti: “Iwe sindiwe woyenera kukapereka uthenga lero, udzapereka uthenga tsiku lina. Lero usakapereke uthenga chifukwa chakuti mwana wa mfumu wafa.”+ 21 Ndiyeno Yowabu anauza Mkusi+ kuti: “Pita ukauze mfumu zimene waona.” Pamenepo Mkusiyo anaweramira Yowabu ndi kuyamba kuthamanga. 22 Tsopano Ahimazi mwana wa Zadoki anauzanso Yowabu kuti: “Chilichonse chichitike, chonde ndiloleni inenso ndithamange kutsatira Mkusiyu.” Koma Yowabu anati: “N’chifukwa chiyani iwenso ukufuna kuthamanga mwana wanga pamene ulibe uthenga woti ukanene?” 23 Iye anapitiriza kunena kuti: “Chilichonse chichitike, ndiloleni ndithamange.” Choncho Yowabu anati: “Thamanga!” Pamenepo Ahimazi anayamba kuthamanga kulowera njira ya ku Chigawo*+ ndipo kenako anamudutsa Mkusi uja.

24 Tsopano Davide anali atakhala pakati pa zipata ziwiri.+ Pa nthawiyi mlonda+ anakwera padenga la mpanda kuchipata. Ndiyeno atakweza maso anaona munthu akuthamanga ali yekha. 25 Choncho mlondayo anaitana mfumu ndi kuiuza zimenezo. Pamenepo mfumuyo inati: “Ngati ali yekha, ndiye kuti akudzanena uthenga.” Munthu uja anali kubwera ndithu, ndipo pang’ono ndi pang’ono anali kuyandikira. 26 Kenako mlonda uja anaonanso munthu wina akuthamanga. Ndiyeno mlondayo anaitana mlonda wa pachipata ndi kumuuza kuti: “Taona! Munthu winanso akuthamanga ali yekha.” Pamenepo mfumu inati: “Ameneyunso akubweretsa uthenga.” 27 Ndiyeno mlondayo anapitiriza kunena kuti: “Ndikuona kuti kathamangidwe ka munthu woyambayu kakufanana ndi kathamangidwe+ ka Ahimazi+ mwana wa Zadoki.” Atatero, mfumu inati: “Ahimazi ndi munthu wabwino,+ ndipo uthenga umene wabweretsa uyenera kukhala wabwino.”+ 28 Kenako Ahimazi anaitana mfumu ndi kuiuza kuti: “Zonse zili bwino!” Atatero anagwada pamaso pa mfumu ndi kuwerama. Ndiyeno anati: “Adalitsike+ Yehova Mulungu wanu, amene wapereka+ amuna amene anatambasula manja awo ndi kuukira inu mbuyanga mfumu!”

29 Koma mfumu inati: “Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino?” Poyankha Ahimazi anati: “Pamene Yowabu anali kutuma mtumiki wa mfumu ndi ine mtumiki wanu, ndinaona chipwirikiti chachikulu, koma sindinadziwe chimene chinali kuchitika.”+ 30 Pamenepo mfumu inati: “Patuka, ima pambalipa.” Choncho anapatuka ndi kuima pambali.

31 Kenako Mkusi+ uja anafika, ndi kuyamba kunena kuti: “Ndabweretsa uthenga mbuyanga mfumu, pakuti Yehova wakuweruzani lero kuti akulanditseni m’manja mwa anthu onse okuukirani.”+ 32 Koma mfumu inafunsa Mkusiyo kuti: “Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino?” Poyankha Mkusiyo anati: “Adani anu mbuyanga mfumu ndi anthu onse ofuna kukuchitirani zoipa akhale ngati mnyamatayo.”+

33 Pamenepo mfumu inasokonezeka ndipo inakwera m’chipinda cha padenga+ cha pachipata ndi kuyamba kulira. Mfumu inali kuyenda n’kumanena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga+ Abisalomu! Haa! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine m’malo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+

19 Patapita nthawi, uthenga unafika kwa Yowabu kuti: “Mfumu ikulira, ikupitiriza kulirira Abisalomu.”+ 2 Choncho tsiku limenelo chipulumutso chinasanduka nthawi yoti anthu onse alire maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti: “Mfumu yakhumudwa ndi imfa ya mwana wake.” 3 Ndipo tsiku limenelo anthu anayamba kulowa mumzinda+ mozemba ngati mmene anthu amazembera chifukwa cha manyazi akathawa kunkhondo. 4 Ndiyeno mfumu inaphimba nkhope yake, ndipo inapitiriza kulira mokweza mawu kuti: “Mwana wanga Abisalomu! Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+

5 Pamapeto pake, Yowabu anafika kunyumba ya mfumu ndi kuiuza kuti: “Lero mwachititsa manyazi nkhope za atumiki anu onse, amene lero apulumutsa moyo wanu+ komanso moyo wa ana anu aamuna,+ ana anu aakazi,+ akazi anu+ ndi adzakazi anu,+ 6 mwa kukonda anthu odana nanu ndi kudana ndi anthu okukondani. Lero mwasonyeza kuti akulu ndi atumiki alibe ntchito kwa inu, chifukwa ine ndikudziwa bwino kuti Abisalomu akanakhala ndi moyo koma ena tonsefe n’kufa, pamenepo zikanakhala bwino kwa inu. 7 Tsopano nyamukani, mutuluke kukalankhula ndi atumiki anu ndi kuwalimbikitsa,+ chifukwa ngati simupita kukalankhula nawo, ndithu ndikulumbira pali Yehova, sipapezeka munthu wogona kuno lero.+ Zimenezi zikhala zoipa kwambiri kwa inu kuposa zoipa zonse zimene mwakumana nazo kuyambira pa ubwana wanu mpaka pano.” 8 Choncho mfumu inanyamuka ndi kukakhala kuchipata.+ Zitatero uthenga unapita kwa anthu onse kuti: “Mfumu yakhala kuchipata.” Pamenepo anthu onse anayamba kubwera kwa mfumu.

Koma Aisiraeli onse amene anagonjetsedwa, aliyense anathawira kunyumba yake.+ 9 Ndiyeno anthu onse anayamba kukangana m’mafuko onse a Isiraeli kuti: “Mfumuyi ndi imene inatilanditsa m’manja mwa adani athu,+ ndipo ndi mfumu yomweyi imene inatipulumutsa m’manja mwa Afilisiti. Tsopano yachoka m’dziko lino kuthawa Abisalomu.+ 10 Koma Abisalomu amene tinamudzoza kukhala mtsogoleri wathu+ wafa kunkhondo.+ Nanga n’chifukwa chiyani simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere?”+

11 Ndiyeno Mfumu Davide inatumiza uthenga kwa Zadoki+ ndi Abiyatara+ ansembe kuti: “Lankhulani ndi akulu a Yuda+ kuti, ‘N’chifukwa chiyani inu nokha simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere kunyumba yake, pamene Aisiraeli onse atumiza uthenga kwa mfumu kumene ikukhala? 12 Inu ndinu abale anga, ndinu fupa langa ndi mnofu wanga.+ Ndiye n’chifukwa chiyani inu nokha simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere?’ 13 Amasa mumuuze kuti,+ ‘Kodi iwe sindiwe fupa langa ndi mnofu wanga? Mulungu andilange mowirikiza+ ngati sudzakhala mtsogoleri wa gulu langa lankhondo nthawi zonse m’malo mwa Yowabu.’”+

14 Pamenepo mitima ya amuna onse a Yuda inakopeka ndipo anamvana chimodzi,+ moti anatumiza uthenga kwa mfumu kuti: “Bwererani, inuyo pamodzi ndi atumiki anu onse.”

15 Ndiyeno mfumu inayamba kubwerera kwawo ndipo inafika ku Yorodano. Pamenepo anthu a Yuda anafika ku Giligala+ kuti apite kukakumana ndi mfumu ndi kuiperekeza pamene inali kuwoloka mtsinje wa Yorodano. 16 Kenako Simeyi+ mwana wa Gera,+ wa fuko la Benjamini, wochokera ku Bahurimu,+ pamodzi ndi amuna a ku Yuda anapita mofulumira kukakumana ndi Mfumu Davide. 17 Iye anali ndi amuna 1,000 ochokera ku Benjamini. (Analinso ndi Ziba+ mtumiki wa nyumba ya Sauli pamodzi ndi ana ake 15+ ndi atumiki ake 20. Iwo anakwanitsa kukafika ku Yorodano mfumu isanafike. 18 Atafika kumeneko, anawolokera tsidya lina+ kuti akawolotse anthu a m’banja la mfumu ndi kuchita zabwino pamaso pake.) Koma mfumu itatsala pang’ono kuwoloka Yorodano, Simeyi mwana wa Gera, anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.+ 19 Ndiyeno anauza mfumu kuti: “Mbuyanga mfumu, musandione ngati munthu wolakwa. Musakumbukire ndi kuikira kumtima cholakwa chimene ine mtumiki wanu ndinachita+ tsiku lija limene inu mbuyanga mfumu munatuluka mu Yerusalemu.+ 20 Pakuti ine mtumiki wanu ndikudziwa bwino kuti ndinachimwa. Tsopano lero ndine woyamba m’nyumba yonse ya Yosefe+ kubwera kuno kudzakumana ndi inu mbuyanga mfumu.”

21 Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya+ anayankha kuti: “Pa zimene wanenazi, kodi Simeyi sakuyenera kuphedwa chifukwa chotemberera wodzozedwa wa Yehova?”+ 22 Koma Davide anati: “Ndili nanu chiyani+ inu ana a Zeruya kuti lero mukhale otsutsana+ nane? Kodi mu Isiraeli muyenera kuphedwa munthu aliyense lero?+ Kodi ine sindikudziwa bwino kuti lero ndine mfumu ya Isiraeli?” 23 Kenako mfumu inauza Simeyi kuti: “Suufa.” Pamenepo mfumu inamulumbirira.+

24 Koma Mefiboseti,+ mdzukulu wake wa Sauli, anabwera kudzaonana ndi mfumu. Iye sanasamalire mapazi ake,+ kumeta ndevu zake zapamlomo+ kapena kuchapa zovala zake kuchokera tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere. 25 Ndiyeno zinachitika kuti, atafika ku Yerusalemu kukakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?” 26 Poyankha anati: “Mbuyanga mfumu, mtumiki wanga ndi amene anandipusitsa. Ine mtumiki wanu+ ndinanena kuti, ‘Ndiikireni chishalo pabulu wamkazi kuti ndikwerepo ndi kupita pamodzi ndi mfumu,’ pakuti ine mtumiki wanu ndine wolumala.+ 27 Choncho mtumiki wangayo anandinenera+ ine mtumiki wanu miseche kwa inu mbuyanga mfumu. Koma inu mbuyanga mfumu muli ngati mngelo+ wa Mulungu woona, motero chitani zimene zili zabwino kwa inu. 28 Pakuti kwa inu mbuyanga mfumu, nyumba yonse ya bambo anga ikanayenera kuwonongedwa, koma m’malomwake mwaika ine mtumiki wanu pakati pa anthu amene akudya chakudya patebulo+ la mfumu. Ndiye ndili ndi chifukwa chanji chomveka chopitirizira kudandaula+ kwa inu mfumu?”

29 Komabe mfumu inamuuza kuti: “N’chifukwa chiyani ukupitiriza kulankhula zonsezi? Ine ndikuti, iwe ndi Ziba mugawane mundawo.”+ 30 Pamenepo Mefiboseti anauza mfumu kuti: “Musiyeni atenge munda wonsewo,+ popeza kuti tsopano inu mbuyanga mfumu mwabwerera kunyumba yanu mu mtendere.”

31 Ndiyeno Barizilai+ Mgiliyadi nayenso anatsika kuchokera ku Rogelimu. Iye anapita ku Yorodano pamodzi ndi mfumu. Barizilai anaperekeza mfumu mpaka kukafika ku Yorodano. 32 Barizilai anali wokalamba kwambiri pakuti anali ndi zaka 80.+ Pamene mfumu inali kukhala ku Mahanaimu,+ Barizilai anali kuipatsa chakudya pakuti iye anali munthu wolemera kwambiri.+ 33 Ndiyeno mfumu inauza Barizilai kuti: “Tiye tiwolokere ku Yerusalemu ndipo tizikadya chakudya pamodzi.”+ 34 Koma Barizilai anauza mfumu kuti: “Kodi masiku a moyo wanga atsala angati kuti ndipite ku Yerusalemu pamodzi ndi mfumu? 35 Ine lero ndili ndi zaka 80.+ Kodi ine mtumiki wanu ndingasiyanitse chabwino ndi choipa kapena kumva kukoma kwa zimene ndadya ndi kumwa?+ Kodi ine ndingathenso kumva+ mawu a amuna ndi akazi oimba?+ Ndiye ine mtumiki wanu ndikhalirenji mtolo wolemetsa+ kwa inu mbuyanga mfumu? 36 Ine mtumiki wanu ndangokuperekezani mtunda waufupi kudzafika kuno ku Yorodano, ndiye n’chifukwa chiyani inu mfumu mukundipatsa mphoto imeneyi?+ 37 Ndiloleni chonde ine mtumiki wanu ndibwerere, ndikafere+ mumzinda wa kwathu pafupi ndi manda a bambo anga ndi mayi anga.+ Koma ndikupereka mtumiki wanu Chimamu.+ Muloleni ameneyu awoloke nanu pamodzi mbuyanga mfumu, ndipo mumuchitire zimene zili zabwino kwa inu.”

38 Pamenepo mfumu inati: “Chimamu awoloka nane pamodzi, ndipo ine ndimuchitira zimene zili zabwino kwa iwe. Chilichonse chimene udzasankha kuti ine ndikuchitire, ine ndidzachita.” 39 Tsopano anthu onse anayamba kuwoloka Yorodano, ndipo mfumu nayonso inawoloka. Koma mfumu inapsompsona+ Barizilai ndi kumudalitsa,+ kenako Barizilai anabwerera kwawo. 40 Pamene mfumu inali kuwolokera ku Giligala,+ Chimamu nayenso anawoloka nayo pamodzi. Anthu onse a Yuda ndi hafu ya anthu a Isiraeli nawonso anawoloka kuti ayende pamodzi ndi mfumu.

41 Pamenepo anthu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “N’chifukwa chiyani+ abale athu a ku Yuda akubweretsani mozemba inu mfumu Davide, pamodzi ndi banja lanu ndi anthu onse amene anali ndi inu kutsidya la Yorodano?”+ 42 Pamenepo anthu a ku Yuda anayankha anthu a ku Isiraeli kuti: “Chifukwa chakuti mfumuyi ndi wachibale wathu wapafupi.+ N’chifukwa chiyani inu mwakwiya nazo zimenezi? Kodi ife tadya zinthu zilizonse za mfumu kapena kulandira mphatso?”

43 Koma anthu a ku Isiraeli anayankha anthu a ku Yuda kuti: “Ifetu tili ndi mafuko 10 mu ufumu umenewu.+ Choncho mu ufumu wa Davide tilitu ndi mphamvu zambiri kuposa inu. Ndiyeno n’chifukwa chiyani mukutinyoza chotero, ndipo kodi ife sitinayenera kukhala patsogolo+ pobweretsa mfumu yathu?” Koma mawu a anthu a ku Yuda anali aukali kwambiri kuposa a anthu a ku Isiraeli.

20 Tsopano panali munthu wina wopanda pake+ dzina lake Sheba,+ mwana wamwamuna wa Bikiri, wafuko la Benjamini. Iye analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi kunena kuti: “Tilibe gawo mwa Davide, ndipo tilibe cholowa mwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu+ yake!” 2 Pamenepo anthu onse a Isiraeli anayamba kuchoka kwa Davide ndi kutsatira Sheba mwana wa Bikiri.+ Koma anthu a ku Yuda, kuyambira ku Yorodano mpaka ku Yerusalemu anamamatira mfumu yawo.+

3 Patapita nthawi, Davide anafika kunyumba yake ku Yerusalemu.+ Ndiyeno mfumuyo inatenga akazi 10+ aja, adzakazi amene anawasiya kuti azisamalira nyumba yake, ndipo anawatsekera m’nyumba ina koma anapitiriza kuwapatsa chakudya. Iye sanagone nawonso,+ koma anawatsekerabe kufikira tsiku la kufa kwawo. Iwo anakhala akazi amasiye mwamuna wawo ali moyo.

4 Tsopano mfumu inauza Amasa+ kuti: “Ndisonkhanitsire anthu a mu Yuda m’masiku atatu, ndipo iwe uime pano.” 5 Choncho Amasa anapita kukasonkhanitsa anthu a mu Yuda, koma anabwera mochedwa kupitirira nthawi imene anamuikira. 6 Ndiyeno Davide anauza Abisai+ kuti: “Tsopano Sheba+ mwana wamwamuna wa Bikiri atisautsa kwambiri kuposa Abisalomu.+ Iweyo utenge atumiki+ a mbuye wako ndi kumuthamangitsa kuti asapeze mizinda ya mipanda yolimba kwambiri ndi kutizemba ife tikuona.” 7 Choncho asilikali a Yowabu,+ Akereti,+ Apeleti+ ndi amuna onse amphamvu anayamba kumuthamangitsa. Iwo anatuluka mu Yerusalemu ndi kuthamangitsa Sheba mwana wa Bikiri. 8 Pamene anali pafupi ndi mwala waukulu umene uli ku Gibeoni,+ Amasa+ anabwera kudzakumana nawo. Tsopano Yowabu anali atavala malaya ankhondo ndi lamba. Iye anali ataika lupanga m’chimake ndi kulipachika m’chiuno mwake. Atayandikira Amasa, lupangalo linagwa pansi.

9 Ndiyeno Yowabu anafunsa Amasa kuti: “Kodi zili bwino m’bale wanga?”+ Kenako dzanja lamanja la Yowabu linagwira ndevu za Amasa kuti amupsompsone.+ 10 Koma Amasa sanachenjere ndi lupanga limene linali m’manja mwa Yowabu. Choncho Yowabuyo anamubaya+ nalo m’mimba ndipo matumbo ake anakhuthukira pansi, moti sanachite kumubaya kawiri. Chotero Amasa anafa. Pamenepo Yowabu ndi Abisai m’bale wake anathamangitsa Sheba mwana wa Bikiri.

11 Zitatero, mmodzi mwa anyamata a Yowabu anaimirira pafupi ndi Amasa ndipo anali kunena kuti: “Aliyense amene amagwirizana ndi Yowabu ndiponso aliyense wa Davide+ atsatire Yowabu!” 12 Ankachita izi Amasa ali chigonere pamagazi ake,+ pakati pa msewu waukulu. Mwamuna uja ataona kuti anthu onse akuima chilili, anakoka Amasa kumuchotsa pamsewu ndi kumuika patchire. Kenako anamuphimba ndi chovala pakuti anaona kuti aliyense amene anali kufika pamenepo anali kuima chilili.+ 13 Atangomuchotsa pamsewupo, munthu aliyense anali kudutsa pamenepo kutsatira Yowabu pothamangitsa Sheba+ mwana wa Bikiri.

14 Tsopano Sheba anadutsa pakati pa mafuko onse a Isiraeli kupita kumzinda wa Abele wa ku Beti-maaka.+ Nawonso Abikiri onse anasonkhana ndi kuyamba kumuthamangitsa.

15 Anthuwo anafika ndi kumuzungulira ali mumzinda+ wa Abele wa ku Beti-maaka. Iwo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo* ndi mzindawo. Anthu onse amene anali ndi Yowabu anali kukumba pansi pa mpandawo kuti augwetse. 16 Ndiyeno mkazi wina wanzeru+ mumzindawo anayamba kufuula kuti: “Tamverani amuna inu, tamverani! Chonde muuzeni Yowabu kuti abwere pafupipa kuti ndilankhule naye.” 17 Choncho Yowabu anayandikira ndipo mkaziyo anati: “Kodi ndiwe Yowabu?” Pamenepo Yowabu anayankha kuti: “Inde, ndine.” Pamenepo mkaziyo anati: “Tamvera mawu a kapolo wako wamkazi.”+ Yowabu anayankha kuti: “Ndikumvetsera.” 18 Ndiyeno mkaziyo ananena kuti: “Nthawi zakale aliyense anali kunena kuti, ‘Akafunsire nzeru ku Abele, ndipo adzapezadi njira yothetsera nkhani yake.’ 19 Ine ndikuimira anthu ofuna mtendere+ ndi okhulupirika+ a mu Isiraeli. Iwe ukufuna kupha mzinda+ ndi mayi mu Isiraeli. N’chifukwa chiyani ukufuna kuwononga+ cholowa+ cha Yehova?” 20 Pamenepo Yowabu anayankha kuti: “Ine sindingawononge ndi kufafaniza mzindawu, n’zosatheka zimenezo. 21 Nkhani sili choncho ayi, koma mumzinda wanu muli munthu wochokera kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Sheba+ mwana wa Bikiri, amene waukira Mfumu Davide.+ Choncho anthu inu m’perekeni iye yekhayo+ m’manja mwathu, ndipo ine ndidzachoka kumzinda+ uno.” Pamenepo mkaziyo anauza Yowabu kuti: “Tikuponyerani mutu+ wake kuchokera pamwamba pa mpanda!”

22 Nthawi yomweyo, mkaziyo anapita mwa nzeru+ zake kwa anthu onse, ndipo anthuwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri ndi kuuponya kwa Yowabu. Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ moti anthu onse anabalalika kuchoka kumzindawo ndi kupita kwawo. Yowabu nayenso anabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.

23 Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lonse lankhondo+ la Isiraeli. Benaya+ mwana wa Yehoyada+ anali kutsogolera Akereti+ ndi Apeleti.+ 24 Adoramu+ anali kutsogolera anthu olembedwa ntchito yokakamiza, ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 25 Seva+ anali mlembi,+ ndipo Zadoki+ ndi Abiyatara+ anali ansembe. 26 Ira Myairi anakhalanso wansembe*+ wa Davide.

21 Tsopano m’masiku a Davide kunagwa njala+ zaka zitatu zotsatizana. Choncho Davide anafunsira kwa Yehova, ndipo Yehova anamuuza kuti: “Sauli pamodzi ndi nyumba yake ali ndi mlandu wa magazi chifukwa anapha Agibeoni.”+ 2 Choncho mfumu inaitana Agibeoni+ ndi kulankhula nawo. (Agibeoni sanali ana a Isiraeli koma otsala mwa Aamori.+ Ana a Isiraeli analumbira kwa Aamori,+ koma Sauli anali kufuna kuwapha+ onse chifukwa chakuti iye anali kuchitira nsanje+ ana a Isiraeli ndi ana a Yuda.) 3 Ndiyeno Davide anafunsa Agibeoni kuti: “Ndikuchitireni chiyani ndipo ndipereke chiyani kuti ndiphimbe tchimo+ limeneli, kuti inu mudalitse cholowa+ cha Yehova?” 4 Choncho Agibeoni anamuyankha kuti: “Sitikufuna siliva kapena golide+ pa nkhani ya Sauli ndi nyumba yake, komanso tilibe ufulu wopha munthu mu Isiraeli.” Ndiyeno Davide anati: “Chilichonse chimene mukufuna ndikuchitirani.” 5 Pamenepo iwo anauza mfumu kuti: “Tikufuna kuti munthu amene anapulula anthu athu,+ ndi kutikonzera chiwembu+ chotiwononga kuti tisapezeke m’dera lililonse la Isiraeli, 6 mutipatse ana ake aamuna 7,+ ndipo tionetse+ mitembo yawo kwa Yehova mwa kuipachika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, munthu amene Yehova+ anamusankha kukhala mfumu.” Pamenepo mfumu inati: “Ndiwapereka m’manja mwanu.”

7 Koma mfumu inamvera chisoni Mefiboseti+ mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha lumbiro+ limene Davideyo ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pakati pawo pamaso pa Yehova. 8 Chotero mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, amene anali ana awiri aamuna a Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya, amene Rizipayo anaberekera Sauli. Anatenganso ana aamuna asanu a Mikala,*+ mwana wamkazi wa Sauli, amene anaberekera Adiriyeli,+ mwana wa Barizilai Mmeholati. 9 Iye anawapereka m’manja mwa Agibeoni, ndipo Agibeoniwo anaonetsa mitembo ya ana aamuna a Sauliwo kwa Yehova+ paphiri, moti onse 7 anafera limodzi. Iwo anaphedwa m’masiku oyambirira a nyengo yokolola, kuchiyambi kwa nyengo yokolola balere.+ 10 Koma Rizipa mwana wamkazi wa Aya+ anatenga chiguduli+ ndi kuchiyala pamwala kuti azikhala pamenepo, kuyambira kuchiyambi kwa nyengo yokolola kufikira pamene mvula inagwa pamitemboyo kuchokera kumwamba.+ Iye sanalole mbalame+ zam’mlengalenga kutera pamitemboyo masana, ndipo usiku sanalole zilombo zakutchire+ kufikapo.

11 Patapita nthawi, Davide anauzidwa+ zimene Rizipa mwana wa Aya, mdzakazi wa Sauli anachita. 12 Chotero Davide anapita kukatenga mafupa a Sauli+ ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-giliyadi.+ Anthuwo ndiwo anaba mitembo ya Sauli ndi Yonatani m’bwalo la mzinda wa Beti-sani,+ kumene Afilisiti anali ataipachika,+ tsiku limene anapha Sauli paphiri la Giliboa.+ 13 Iye anabwera ndi mafupa a Sauli ndi mafupa a Yonatani mwana wake. Atatero anasonkhanitsanso mafupa a anthu amene anaonetsedwa aja.+ 14 Kenako anaika mafupa a Sauli ndi Yonatani mwana wake m’dziko la Benjamini ku Zela+ m’manda a Kisi+ bambo ake, kuti achite zonse zimene mfumu inalamula. Izi zitachitika, Mulungu anamvetsera kuchonderera kwawo kuti amvere chisoni dziko lawo.+

15 Ndiyeno Afilisiti+ anabwera kudzachita nkhondo ndi Isiraeli. Pamenepo Davide ndi atumiki ake anapita komweko n’kumenyana ndi Afilisiti, ndipo Davide anatopa. 16 Zitatero, Isibi-benobi mmodzi wa mbadwa za Arefai,+ amene anali ndi mkondo wamkuwa wolemera+ masekeli 300,* amenenso anali ndi lupanga latsopano m’chiuno mwake, anaganiza zoti aphe Davide. 17 Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya anathandiza+ Davide ndipo anakantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti: “Simudzapitanso ndi ife kunkhondo,+ chifukwa mungazimitse+ nyale+ ya Isiraeli!”

18 Ndiyeno pambuyo pa nkhondo imeneyi panabukanso nkhondo ndi Afilisiti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai+ Mhusati+ anapha Safi, amene anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+

19 Kenako panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti ku Gobu, ndipo Elihanani+ mwana wa Yaare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu.+

20 Panabukanso nkhondo ina ku Gati,+ pa nthawi imene kunali munthu wa msinkhu waukulu modabwitsa. Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24 zonse pamodzi. Ameneyunso anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+ 21 Iye anali kutonza+ ndi kuderera Isiraeli. Pamapeto pake Yonatani+ mwana wa Simeyi,+ m’bale wake wa Davide, anamupha.

22 Anthu anayi amenewa anali mbadwa za Arefai ku Gati.+ Iwo anaphedwa ndi dzanja la Davide ndi la atumiki ake.+

22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamulanditsa kwa adani ake+ onse ndiponso m’manja mwa Sauli.+ 2 Iye anati:

“Yehova ndiye thanthwe langa,+ malo anga achitetezo+ ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+

 3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa.+ Ine ndidzathawira kwa iye,

Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga+ ya chipulumutso ndi malo anga okwezeka achitetezo.+

Iye ndi malo anga othawirako,+ Mpulumutsi wanga.+ Mumandipulumutsa ku chiwawa.+

 4 Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+

Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+

 5 Pakuti mafunde akupha anandizungulira.+

Panali chikhamu cha anthu opanda pake amene anali kundiopseza.+

 6 Zingwe za Manda* zinandizungulira.+

Ndinakumana ndi misampha ya imfa.+

 7 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+

Ndinaitana Mulungu wanga.+

Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+

Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+

 8 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+

Maziko a kumwamba anagwedezeka.+

Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+

 9 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+

Makala onyeka anatuluka mwa iye.+

10 Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+

Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake.+

11 Iye anafika atakwera pakerubi+ wouluka.

Anaonekera pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+

12 Kenako anaika mdima momuzungulira ngati misasa,+

Anaika madzi akuda ndi mtambo wakuda.+

13 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.+

14 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+

Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake.+

15 Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+

Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+

16 Ndipo ngalande za pansi pa nyanja zinaonekera,+

Maziko a dziko lapansi+ anakhala poonekera,

Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwake.+

17 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+

Anandivuula m’madzi akuya.+

18 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+

Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+

19 Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+

Koma Yehova anandichirikiza.+

20 Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+

Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+

21 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+

Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+

22 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+

Sindinachoke kwa Mulungu wanga.+ Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.

23 Pakuti zigamulo+ zake zonse zili pamaso panga.

Ndipo sindidzapatuka pa malamulo ake.+

24 Ndidzakhalabe wopanda cholakwa+ pamaso pake,

Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+

25 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+

Andibwezere mogwirizana ndi kukhala kwanga woyera pamaso pake.+

26 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+

Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+

27 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+

Kwa munthu wopotoka maganizo mudzachita zinthu ngati wopusa.+

28 Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa.+

Koma mumatsutsa odzikweza, kuti muwatsitse.+

29 Inu Yehova ndinu nyale yanga,+

Ndipo Yehova ndiye amandiunikira pamene ndili mu mdima.+

30 Pakuti ndi thandizo lanu ndingathamangitse gulu la achifwamba.+

Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+

31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+

Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+

Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+

32 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+

Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+

33 Mulungu woona ndiye malo anga otetezeka kwambiri,+

Ndipo adzasalaza njira yanga.+

34 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+

Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+

35 Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo.+

Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+

36 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+

Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.+

37 Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga.+

Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+

38 Ndidzathamangitsa adani anga kuti ndiwafafanize,

Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+

39 Ndidzawawononga onse ndi kuwaphwanya zibenthuzibenthu+ kuti asadzukenso.+

Iwo adzagwa pansi ndipo ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+

40 Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.+

Mudzakomola ondiukira.+

41 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+

Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+

42 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+

Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+

43 Ndidzawapera kukhala ngati fumbi la padziko lapansi.

Ndidzawapondaponda ngati matope a mumsewu,+

Ndipo ndidzawasasantha.

44 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+

Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu yonse.+

Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+

45 Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+

Anthu adzamvetsera mawu anga ndi kuwatsatira.+

46 Alendo adzatha mphamvu,

Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+

47 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+

Mulungu wanga, thanthwe limene limandipulumutsa likhale lokwezeka.+

48 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga,+

Iye amaika mitundu ya anthu kunsi kwa mapazi anga.+

49 Iye amandichotsa pakati pa adani anga.+

Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+

Mudzandilanditsa kwa munthu wochita zachiwawa.+

50 N’chifukwa chake ndidzayamika inu Yehova pakati pa mitundu.+

Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+

51 Ndidzaimbira Iye wochita ntchito zazikulu zachipulumutso kwa mfumu yake,+

Iye wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+

Kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.”+

23 Mawu omaliza amene Davide ananena ndi awa:+

“Mawu a Davide mwana wa Jese,+

Mawu a munthu wamphamvu amene anakwezedwa pamwamba,+

Wodzozedwa+ wa Mulungu wa Yakobo,

Munthu wosangalatsa wotchulidwa m’nyimbo zokoma+ za Isiraeli.

 2 Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa,+

Ndipo mawu ake anali palilime langa.+

 3 Mulungu wa Isiraeli analankhula,

Thanthwe la Isiraeli linandiuza kuti,+

‘Munthu wolamulira anthu akakhala wolungama,+

N’kumalamulira moopa Mulungu,+

 4 Ulamuliro wake umakhala ngati kuwala kwa m’mawa pamene dzuwa lawala,+

M’mawa wopanda mitambo.

Umakhala ngati msipu womera padziko mvula ikakata, dzuwa n’kuwala.’+

 5 Kodi si mmene nyumba yanga ilili kwa Mulungu?+

Chifukwa chakuti anachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+

Analikonza bwino ndipo n’lotetezeka.+

Chifukwa ndilo chipulumutso changa+ ndi chondikondweretsa,

Kodi chimenechi sindicho chifukwa chake adzakulitsa panganoli?+

 6 Koma anthu onse opanda pake+ amawakankhira kutali+ ngati zitsamba zaminga.+

Pakuti zitsamba zamingazo sizigwiridwa ndi manja pozichotsa.

 7 Munthu akamazigwira

Ayenera kukhala ndi zida zachitsulo ndi mkondo,

Ndipo zidzatenthedwa ndi moto n’kupseratu.”+

8 Mayina a amuna amphamvu+ a Davide ndi awa: Yosebu-basebete+ Mtahakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 800 ulendo umodzi. 9 Womutsatira anali Eleazara+ mwana wa Dodo+ mwana wa Ahohi. Iye anali mmodzi mwa amuna atatu amphamvu amene anali ndi Davide pamene anatonza Afilisiti. Iwo anasonkhana kumeneko kuti amenye nkhondo, ndipo amuna a Isiraeli anali atathawa.+ 10 Eleazara ndi amene anaimirira ndipo anali kupha Afilisiti mpaka dzanja lake linatopa, koma anagwirabe lupanga+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu pa tsiku limenelo.+ Koma anthu ena onse anamutsatira pambuyo pake kuti avule zovala za anthu ophedwawo.+

11 Womutsatira anali Shama, mwana wamwamuna wa Age Mharari.+ Tsopano Afilisiti anasonkhana pamodzi ku Lehi, kumene kunali munda wodzaza ndi mphodza.+ Kumeneko anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo. 12 Koma iye anaima pakati pa kachigawo ka mundako ndi kukalanditsa ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti tsiku limenelo Yehova anapereka chipulumutso chachikulu.+

13 Ndiyeno pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuphanga la Adulamu.+ Apa n’kuti Afilisiti atamanga msasa wa mahema m’chigwa cha Arefai.+ 14 Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali+ a Afilisiti uli ku Betelehemu. 15 Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chili pachipata!”+ 16 Pamenepo amuna atatu amphamvu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma iye anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+ 17 Ndiyeno iye anati: “Sindingachite zimenezo+ inu Yehova! Kodi ndimwe magazi+ a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Choncho iye sanavomere kumwa madziwo.

Izi n’zimene amuna atatu amphamvuwo anachita.

18 Koma Abisai,+ m’bale wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu 30 amenewo. Iye ananyamula mkondo ndi kupha nawo anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+ 19 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, ndipo anali mtsogoleri wawo, komabe sanafanane ndi amuna atatu oyamba aja.+

20 Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa.+ 21 Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Ngakhale kuti Mwiguputoyo anali ndi mkondo m’manja mwake, Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+ 22 Zimenezi n’zimene Benaya+ mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati amuna atatu amphamvu aja.+ 23 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, sanafanane ndi amuna atatu aja. Koma Davide anamuika kukhala msilikali wake womulondera.+

24 Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu anali m’gulu la amuna 30 aja. M’gululi munalinso Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, 25 Shama+ Mharodi, Elika Mharodi, 26 Helezi+ Mpaliti, Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa, 27 Abi-ezeri+ Muanatoti,+ Mebunai Mhusati,+ 28 Zalimoni Mwahohi,+ Maharai+ Mnetofa, 29 Helebi+ mwana wa Bana Mnetofa, Itai+ mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la ana a Benjamini, 30 Benaya+ Mpiratoni, Hidai wa kuzigwa* za Gaasi,+ 31 Abi-aliboni Mwaraba, Azimaveti+ M’bahurimu, 32 Eliyaba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,+ 33 Shama Mharari, Ahiyamu+ mwana wa Sarari Mharari, 34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaakati, Eliyamu mwana wa Ahitofeli+ Mgilo, 35 Heziro+ wa ku Karimeli, Paarai Mwarabu, 36 Igali mwana wa Natani+ wa ku Zoba, Bani Mgadi, 37 Zeleki+ Muamoni, Naharai M’beeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, 38 Ira Muitiri,+ Garebi+ Muitiri, 39 ndi Uriya+ Mhiti, onse pamodzi 37.

24 Mkwiyo wa Yehova unayakiranso+ Isiraeli pamene winawake anaukira Isiraeli mwa kulimbikitsa Davide kuti: “Pita ukawerenge+ anthu a Isiraeli ndi Yuda.” 2 Choncho mfumu inauza Yowabu+ mkulu wa magulu ankhondo amene anali naye kuti: “Yendayenda m’mafuko onse a Isiraeli kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Ndipo amuna inu muwerenge anthu+ kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”+ 3 Koma Yowabu anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu awonjezere anthu kuwirikiza nthawi 100 pa kuchuluka kwawo, maso anu inu mbuyanga mfumu akuona. Koma inu mbuyanga mfumu, n’chifukwa chiyani mukufuna kuchita zimenezi?”+

4 Pamapeto pake mawu a mfumu anaposa+ mawu a Yowabu ndi atsogoleri a magulu ankhondo. Choncho Yowabu ndi atsogoleri a magulu ankhondowo anachoka pamaso pa mfumu ndi kupita kukawerenga+ anthu a Isiraeli. 5 Kenako anawoloka Yorodano ndi kumanga msasa ku Aroweli+ kudzanja lamanja la mzinda umene uli pakati pa chigwa,* kuyang’ana kudziko la Agadi+ ndi ku Yazeri.+ 6 Atachoka kumeneko anafika ku Giliyadi+ ndi kudziko la Tatimu-hodisi, ndipo anapitirira mpaka ku Dani-jaana ndi kuzungulira kukafika ku Sidoni.+ 7 Kenako anafika kumzinda wa mpanda wolimba wa Turo+ ndiponso kumizinda yonse ya Ahivi+ ndi Akanani. Pamapeto pake anafika ku Beere-seba+ ku Negebu,+ m’dziko la Yuda. 8 Chotero anayendayenda m’dziko lonse ndipo patatha miyezi 9 ndi masiku 20 anafika ku Yerusalemu. 9 Tsopano Yowabu anapereka chiwerengero chonse+ cha anthu kwa mfumu. Aisiraeli analipo 800,000, amuna amphamvu ogwira lupanga, ndipo amuna a Yuda analipo 500,000.+

10 Davide atawerengadi anthuwo anavutika mumtima mwake.+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano Yehova, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu+ chonde, pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+ 11 Davide atadzuka m’mawa, mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi,+ wamasomphenya wa Davide+ kuti: 12 “Pita, ukauze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndaika zilango zitatu pamaso pako.+ Sankha wekha chimodzi mwa zitatuzi chimene ukufuna kuti ndikuchitire.”’”+ 13 Pamenepo Gadi anapita kwa Davide ndi kumuuza kuti:+ “Kodi m’dziko lanu mubwere njala yaikulu zaka 7,+ kapena muzithawa adani anu akukuthamangitsani miyezi itatu,+ kapena kodi kugwe mliri wa masiku atatu m’dziko lanu?+ Ganizirani mofatsa zoti ndikayankhe kwa Amene wandituma.” 14 Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, tilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+

15 Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli kuyambira m’mawa mpaka nthawi yoikidwiratu, moti pa anthu onse kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba+ panafa anthu 70,000.+ 16 Ndiyeno mngelo+ anali atatambasula dzanja lake kuloza ku Yerusalemu kuti awononge mzindawo. Pamenepo Yehova anamva chisoni+ chifukwa cha tsokalo, choncho anauza mngelo amene anali kupha anthuyo kuti: “Basi pakwanira! Tsopano tsitsa dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ Myebusi.+

17 Ndiyeno Davide atangoona mngelo amene anali kupha anthuyo anauza Yehova kuti: “Tsopano amene ndachimwa ndine, ndipo ine ndi amene ndachita cholakwa, nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Dzanja lanu likhale pa ine+ chonde ndi panyumba ya bambo anga.”

18 Kenako Gadi anafika kwa Davide tsiku limenelo ndi kumuuza kuti: “Pita ukamangire Yehova guwa lansembe pamalo opunthira mbewu a Arauna Myebusi.”+ 19 Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi, mogwirizananso ndi zimene Yehova analamula.+ 20 Arauna atasuzumira panja anaona mfumu ndi atumiki ake akubwera kwa iye. Nthawi yomweyo Arauna anatuluka ndi kugwada+ pamaso pa mfumu ndipo anawerama mpaka nkhope yake pansi.+ 21 Ndiyeno Arauna anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Poyankha Davide anati: “Ndabwera kuti undigulitse+ malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe pamenepo, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa.” 22 Koma Arauna anauza Davide kuti: “Mbuyanga mfumu, tengani+ malowo ndipo mupereke chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Onani, ng’ombe iyi ikhale nsembe yopsereza ndipo chopunthira ndi zipangizo za ng’ombe zikhale nkhuni.+ 23 Ine Arauna ndikupereka chilichonse kwa inu mfumu.” Kenako Arauna anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu asonyeze kuti akukondwera nanu.”+

24 Koma mfumu inauza Arauna kuti: “Iyayi, ineyo ndigula zimenezi.+ Ine sindipereka nsembe zopsereza za nyama kwa Yehova Mulungu wanga popanda kulipira.”+ Choncho Davide anagula+ malo opunthira mbewu ndi ng’ombe ndipo analipira ndalama zokwana masekeli 50 asiliva. 25 Zitatero, Davide anamangira Yehova guwa lansembe+ pamenepo ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Choncho Yehova anamva kuchonderera kwawo,+ moti mliriwo anauthetsa mu Isiraeli.

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”

N’kutheka kuti mawu akuti “zinthu zandivuta,” akusonyeza kuti chinachake chinali chitamuchitikira moti sakanathanso kudziteteza.

Mawu ake enieni, “minda ya zopereka zopatulika.”

Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.

Dzinali limatanthauza, “Malo a Mipeni ya Mwala wa Nsangalabwi.”

Ena amati “kugwaza.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Pa 1Sa 25:44 akutchedwa Paliti.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “saka.”

M’Chiheberi, mawu akuti “Chimulu cha Dothi” ndi mil·lohʹ. Mwina chinali chinyumba chokhala ndi chitetezo champhamvu.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Dzinali limatanthauza, “Ambuye wa Zigumula.”

Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.

M’malo mwa “Geba,” pa 1Mb 14:16 pali dzina lakuti “Gibeoni.”

Dzinali limatanthauza, “Mkwiyo Wophulikira Uza.”

Mawu akuti “nyumba” akutanthauza mzere wa mafumu.

Anali kuzipundula mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wam’mbuyo.

Kapena kuti “nduna zazikulu zotumikira mfumu.”

Pa mawu akuti “tebulo langa,” mipukutu ina imanena kuti “tebulo la Davide,” kapenanso “tebulo la mfumu.” Choncho ena amanena kuti mawu akuti “tebulo langa” ayenera kukhala “tebulo la Davide.” N’kuthekanso kuti Ziba anali kubwereza mawu amene Davide ananena.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti “tsindwi.”

Pa 1Mb 3:5 akutchedwa “Amiyeli.”

Pa Owe 6:32; Owe 7:1; Owe 9:1, 16, 24, 28, akutchedwa “Yerubaala.”

Kutanthauza, “Wamtendere.”

Dzinali limatanthauza, “Wokondedwa ndi Ya.”

Mawu ake enieni, “chifukwa cha Yehova.”

N’kutheka kuti mawu akuti “mzinda wa madzi” akutanthauza malo amene madzi a mumzindawo anali kuchokera.

N’kutheka kuti ameneyu anali fano la mulungu wa Aamoni. M’malemba ena amatchedwa “Moleki” kapena “Milikomu.”

Talente limodzi limeneli ndi makilogalamu 34.

Makeke amenewa sanali ophikidwa mu uvuni ngati mkate, koma ayenera kuti anali ophikidwa m’mafuta ambiri ngati madonasi.

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Umenewu uyenera kuti unali muyezo umene anali kuusunga kunyumba ya mfumu kapena linali sekeli “lachifumu” losiyana ndi sekeli wamba. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa Eks 30:13.

N’zotheka kuti zaka 40 zimenezi akuziwerenga kuchokera pamene Davide anadzozedwa kukhala mfumu. Onani 1Sa 16:13.

Dzinali limatanthauza, “Nyumba Yakutali.”

Apa akunena za amene anatsatira “Itai,” wotchulidwa m’vesi 19.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29.

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 8:18.

Mipukutu ya Targum imati: “Ana aamuna asanu amene Merabu anabereka (amene Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, analera).” Yerekezerani ndi 2Sa 6:23.

Pafupifupi makilogalamu atatu ndi hafu.

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Onani Zakumapeto 5.

Kapena kuti “mapiko a mphepo.”

Kapena kuti, “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena