Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 1 Kings 1:1-22:53
  • 1 Mafumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Mafumu
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Mafumu

Mafumu Woyamba

kapena, malinga ndi Baibulo lachigiriki la Septuagint, MAFUMU WACHITATU

1 Mfumu Davide anali atakalamba+ ndipo anali ndi zaka zambiri. Ankamufunditsa zovala koma sankamva kutentha. 2 Choncho atumiki ake anamuuza kuti: “Mbuyanga mfumu, anthu akufunireni namwali wamng’ono+ woti azisamalira+ inu mfumu. Akhale mlezi+ wanu woti azigona pafupi nanu+ ndipo mbuyanga mfumu muzitenthedwa.”+ 3 Ndiyeno anakafunafuna mtsikana wokongola m’dziko lonse la Isiraeli. Pamapeto pake anapeza Abisagi+ Msunemu+ n’kubwera naye kwa mfumu. 4 Mtsikanayo anali chiphadzuwa+ ndipo anakhala wosamalira mfumu. Mfumuyo sinagonepo naye.

5 Pa nthawi imeneyi Adoniya+ mwana wa Hagiti+ anadzikweza+ n’kumati: “Ineyo ndikhala mfumu yolamulira!”+ Kenako anapangitsa galeta* lake. Analinso ndi amuna okwera pamahatchi,* ndi amuna 50 amene ankathamanga patsogolo pake.+ 6 Bambo ake sanafune kumukhumudwitsa pa nthawi ina iliyonse, choncho sanam’dzudzulepo kuti: “Wachitiranji zinthu m’njira imeneyi?”+ Iye analinso wooneka bwino kwambiri,+ ndipo mayi ake anam’bereka pambuyo pobereka Abisalomu. 7 Iye anayamba kuchitira zinthu limodzi ndi Yowabu mwana wa Zeruya komanso wansembe Abiyatara.+ Iwowa anayamba kumuthandiza Adoniya+ monga otsatira ake. 8 Koma wansembe Zadoki,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, mneneri Natani,+ Simeyi,+ Reyi, ndi amuna amphamvu+ a Davide, sanagwirizane+ ndi Adoniya.

9 Pomaliza Adoniya anapereka nsembe+ za nkhosa, ng’ombe, ndi ana a ng’ombe onenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti umene uli pafupi ndi Eni-rogeli.+ Kumeneko anaitanirako abale ake onse, omwe anali ana a mfumu,+ ndi amuna onse a mu Yuda, omwe anali atumiki a mfumu. 10 Koma mneneri Natani, Benaya, amuna amphamvu a Davide, ndi Solomo m’bale wake sanawaitane. 11 Kenako Natani+ anauza Bati-seba+ mayi wake wa Solomo+ kuti: “Kodi simunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti+ wakhala mfumu koma mbuye wathu Davide sakuzidziwa n’komwe zimenezi? 12 Tsopano mvetserani malangizo amphamvu amene ndikupatseni,+ kuti mupulumutse moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomo.+ 13 Pitani kwa Mfumu Davide mukanene kuti, ‘Kodi si inu mbuyanga mfumu amene munalumbirira ine kapolo wanu kuti: “Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo panga, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu”?+ Nanga n’chifukwa chiyani Adoniya wakhala mfumu?’ 14 Inu muli mkati molankhula ndi mfumuyo, ineyo ndidzabwera pambuyo panu n’kutsimikizira mawu anuwo.”+

15 Zitatero, Bati-seba analowa kuchipinda kumene kunali mfumu.+ Mfumuyo inali yokalamba+ kwambiri ndipo Abisagi+ Msunemu anali kuisamalira. 16 Bati-seba anagwada n’kuweramira pansi+ pamaso pa mfumu. Mfumuyo inati: “Ukufuna kupempha chiyani?”+ 17 Bati-seba anayankha kuti: “Mbuyanga,+ ndinu amene munalumbira pa Yehova Mulungu wanu kwa ine kapolo wanu kuti, ‘Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo pa ine, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu.’+ 18 Koma tsopano onani, Adoniya+ wakhala mfumu ndipo inu mbuyanga mfumu simukuzidziwa n’komwe zimenezi.+ 19 Iye wapereka nsembe zambiri, za ng’ombe zamphongo, ana a ng’ombe onenepa, ndiponso nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu,+ wansembe Abiyatara,+ ndi Yowabu+ mkulu wa asilikali, koma Solomo mtumiki wanu sanamuitane.+ 20 Tsopano maso+ a Aisiraeli onse ali pa inuyo mbuyanga mfumu, kuti muwauze amene akhale pampando wachifumu wa mbuyanga mfumu pambuyo panu.+ 21 Zomwe zidzachitike n’zoti, inuyo mbuyanga mfumu mukadzangogona m’manda limodzi ndi makolo anu,+ ineyo ndi mwana wanga Solomo tidzaoneka ngati olakwa.”

22 Bati-seba ali mkati molankhula ndi mfumuyo, mneneri Natani analowa.+ 23 Nthawi yomweyo anthu anauza mfumu kuti: “Kwabwera mneneri Natani!” Kenako Natani anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.+ 24 Ndiyeno Natani anati: “Mbuyanga mfumu, kodi munanena kuti, ‘Adoniya ndiye adzakhale mfumu pambuyo panga ndipo ndiye amene adzakhale pampando wanga wachifumu’?+ 25 Chifukwatu lero wapita kukapereka nsembe+ zambiri, za ng’ombe zamphongo, ana a ng’ombe onenepa, ndi nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu, akulu a asilikali ndi wansembe Abiyatara.+ Moti panopa ali kumeneko ndipo akudya ndi kumwa pamaso pake n’kumanena kuti, ‘Mfumu Adoniya ikhale ndi moyo wautali!’+ 26 Koma ineyo mtumiki wanu, wansembe Zadoki,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mtumiki wanu, sanatiitane.+ 27 Ngati zimenezi zachokera kwa inu mbuyanga mfumu, ndiye kuti simunandidziwitse ineyo mtumiki wanu,+ za amene ayenera kukhala pampando wachifumu wa mbuyanga mfumu pambuyo panu.”

28 Tsopano Mfumu Davide inayankha kuti: “Amuna inu, ndiitanireni Bati-seba.”+ Choncho Bati-seba analowa n’kuima pamaso pa mfumu. 29 Mfumuyo inalumbira+ kuti: “Pali Yehova+ amene anapulumutsa+ moyo wanga+ m’masautso onse,+ 30 monga momwe ndinakulumbirira pa Yehova Mulungu wa Isiraeli, kuti, ‘Mwana wako Solomo adzakhala mfumu pambuyo panga ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu m’malo mwanga,’ ndi mmene ndichitire lero.”+ 31 Kenako Bati-seba anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ pamaso pa mfumu, n’kunena kuti: “Mbuyanga Mfumu Davide akhale ndi moyo mpaka kalekale!”*+

32 Nthawi yomweyo Mfumu Davide inati: “Amuna inu, ndiitanireni wansembe Zadoki,+ mneneri Natani ndi Benaya+ mwana wa Yehoyada.” Anthuwo anabweradi. 33 Mfumuyo inawauza kuti: “Tengani atumiki+ a mbuye wanu, n’kukweza Solomo mwana wanga panyulu* yanga yaikazi,+ ndipo mupite naye ku Gihoni.+ 34 Kumeneko, wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akam’dzoze+ kukhala mfumu ya Isiraeli. Ndiyeno mukalize lipenga+ ndi kunena kuti, ‘Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali!’+ 35 Ndiye pobwera muzikamulondola, ndipo adzafike kuno n’kukhala pampando wanga wachifumu. Iyeyo adzakhala mfumu m’malo mwanga ndipo ndidzamuika kukhala mtsogoleri wa Isiraeli ndi Yuda.” 36 Nthawi yomweyo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti: “Zikhale momwemo!*+ Yehova, Mulungu wa mbuyanga mfumu, atsimikizire zimenezi.+ 37 Monga momwe Yehova anakhalira ndi inu mbuyanga mfumu,+ akhalenso ndi Solomo+ ndipo achititse mpando wake wachifumu kukhala waukulu+ kuposa mpando wanu wachifumu, mbuyanga Mfumu Davide.”

38 Wansembe Zadoki,+ mneneri Natani,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, Akereti+ ndi Apeleti+ anatsetsereka n’kukakweza Solomo panyulu yaikazi ya Mfumu Davide,+ kenako anapita naye ku Gihoni.+ 39 Tsopano wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta+ m’chihema+ n’kudzoza+ Solomo. Ndiyeno anthuwo anayamba kuliza lipenga ndipo anthu onse anafuula kuti: “Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali!”+ 40 Atatero anthuwo anayamba kumulondola ndipo anali kuimba zitoliro+ ndi kusangalala kwambiri,+ moti nthaka+ inang’ambika chifukwa cha phokoso lawo.

41 Adoniya ndi anthu onse amene anawaitana omwe anali naye limodzi anamva phokosolo atamaliza kudya.+ Yowabu atamva phokoso la lipenga, nthawi yomweyo anati: “Kodi phokoso+ likumveka m’mudzili n’lachiyani?” 42 Akulankhula mawu amenewa, kunabwera Yonatani+ mwana wa wansembe Abiyatara. Ndipo Adoniya anati: “Lowa, uyenera kuti wabweretsa nkhani yabwino+ popeza ndiwe mwamuna wolimba mtima.” 43 Koma Yonatani anamuyankha Adoniya kuti: “Ayi, si nkhani yabwino! Mbuyathu Mfumu Davide waveka Solomo ufumu.+ 44 Choncho mfumu inatuma wansembe Zadoki, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ndipo iwo anakweza Solomo panyulu yaikazi ya mfumu.+ 45 Ndiyeno wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamudzoza ku Gihoni kukhala mfumu.+ Kenako abwerako akusangalala ndipo m’mudzimo muli phokoso lokhalokha. Phokoso limenelo ndi limene munamva lija.+ 46 Komanso, Solomo wakhala pampando wachifumu.+ 47 Kuwonjezera apo, atumiki a mfumu abwera kudzafunira mafuno abwino mbuye wathu Mfumu Davide kuti: ‘Mulungu wanu akulitse dzina la Solomo kuposa dzina lanu ndiponso akweze ufumu wake kuposa ufumu wanu!’+ Kenako mfumuyo inaweramira pabedi.+ 48 Komanso mfumu inati, ‘Adalitsike+ Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene lero wapereka munthu woti akhale pampando wanga wachifumu, ine ndikuona ndi maso anga.’”+

49 Anthu onse oitanidwa amene anali ndi Adoniya anayamba kunjenjemera ndipo anaimirira, aliyense n’kumapita kwawo.+ 50 Adoniya anachita mantha chifukwa cha Solomo. Choncho ananyamuka n’kupita kukagwira nyanga za guwa lansembe.+ 51 Patapita nthawi Solomo anauzidwa kuti: “Adoniya wachita mantha ndi Mfumu Solomo moti wakagwira nyanga za guwa lansembe, ndipo wati, ‘Mfumu Solomo indilumbirire kaye kuti siipha mtumiki wakene ndi lupanga.’” 52 Solomo atamva anati: “Akadzakhala munthu wolimba mtima, ngakhale tsitsi lake limodzi+ silidzathothoka n’kugwera pansi, koma choipa chikadzapezeka mwa iye,+ adzaphedwa.”+ 53 Choncho Mfumu Solomo inatumiza anthu kuti akachotse Adoniya paguwa lansembe lija n’kubwera naye. Kenako Adoniya analowa n’kugwadira Mfumu Solomo. Ndiyeno Solomo anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako.”+

2 Davide atatsala pang’ono kumwalira,+ anaitana mwana wake Solomo n’kumulamula kuti: 2 “Ine ndatsala pang’ono kufa,+ choncho iweyo uchite zinthu mwamphamvu+ ndipo ukhale wolimba mtima.+ 3 Uzimvera Yehova Mulungu wako mwa kuyenda m’njira zake,+ kusunga malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi maumboni* ake, malinga ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Mose.+ Uzitero kuti udzakhale wanzeru m’zochita zako zonse, ndiponso kulikonse kumene udzapite. 4 Komanso kuti Yehova adzakwaniritse mawu ake okhudza ine amene analankhula,+ akuti, ‘Ana ako+ akadzasamalira njira zawo, mwa kuyenda+ mokhulupirika*+ pamaso panga ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+

5 “Iweyo ukudziwa bwino kwambiri zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichita,+ mwa kupha akulu awiri a asilikali a Isiraeli, Abineri+ mwana wa Nera ndi Amasa+ mwana wa Yeteri.+ Mwakutero, anakhetsa magazi+ ankhondo pa nthawi yamtendere. Ndipo anadetsa ndi magazi ankhondo lamba amene anali m’chiuno mwake ndiponso nsapato zimene zinali kuphazi kwake. 6 Iweyo uchite zinthu monga mwa nzeru zako,+ ndipo usalole kuti imvi zake zitsikire ku Manda*+ mwamtendere.+

7 “Ana a Barizilai+ Mgiliyadi uwasonyeze kukoma mtima kosatha. Azikhala pakati pa anthu odyera nawe limodzi patebulo,+ chifukwa anandithandiza+ pa nthawi imene ndinali kuthawa m’bale wako Abisalomu.+

8 “Taona, ukukhala pafupi ndi Simeyi+ wa ku Bahurimu,+ mwana wa Gera M’benjamini. Iyeyu ananditemberera temberero lopweteka+ tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu.+ Ndi iyeyu amene anabwera kudzakumana nane pa Yorodano,+ choncho ndinamulumbirira pamaso pa Yehova kuti: ‘Sindidzakupha ndi lupanga.’+ 9 Tsopano usangomusiya, um’lange,+ poti ndiwe munthu wanzeru+ ndipo ukudziwa bwino zimene uyenera kumuchita. Utsitsire imvi zake+ ku Manda zili ndi magazi.”+

10 Kenako Davide anagona limodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ 11 Davide analamulira Isiraeli zaka 40.+ Ku Heburoni+ analamulira zaka 7,+ ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+

12 Solomo anakhala pampando wachifumu wa Davide bambo ake,+ ndipo m’kupita kwa nthawi, ufumu wake unakhazikika.+

13 Patapita nthawi, Adoniya mwana wa Hagiti anapita kwa Bati-seba,+ amayi a Solomo. Iwo atamuona, anam’funsa kuti: “Kodi mwabwerera mtendere?”+ Iye anayankha kuti: “Inde, ndabwerera mtendere.” 14 Kenako iye anapitiriza kuti: “Ndili nanu mawu.” Ndiyeno Bati-seba anati: “Lankhulani.”+ 15 Adoniya anapitiriza kuti: “Inu mukudziwa bwino kuti ufumu unayenera kukhala wanga, ndipo Aisiraeli onse maso awo anali pa ine kuti ndikhala mfumu.+ Koma ufumuwo unatembenuka n’kukhala wa m’bale wanga, chifukwa Yehova ndiye anam’patsa ufumuwo kuti ukhale wake.+ 16 Tsopano ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanire pempho langa.”+ Choncho Bati-seba anamuyankha kuti: “Lankhulani.” 17 Adoniya anapitiriza kuti: “Chonde, mukauze Mfumu Solomo kuti andipatse Abisagi+ Msunemu+ akhale mkazi wanga. Ndikudziwa kuti inuyo sakakukanirani.” 18 Bati-seba atamva anati: “Chabwino. Ndikakulankhulirani kwa mfumu.”

19 Choncho Bati-seba anapita kwa Mfumu Solomo kuti akauze mfumuyo zofuna za Adoniya.+ Nthawi yomweyo mfumu inaimirira+ kuti ikumane naye ndipo inamuweramira.+ Kenako inakhala pampando wake wachifumu n’kuitanitsa mpando wina ndipo inauika kumbali yake yakumanja kuti amayi a mfumu akhalepo.+ 20 Ndiyeno Bati-seba anati: “Pali kanthu kakang’ono kamodzi kamene ndikufuna kupempha. Musandikanire pempho langa.” Mfumuyo inamuuza kuti: “Pemphani mayi anga, sindikukanirani.” 21 Choncho Bati-seba anapitiriza kuti: “Perekani Abisagi Msunemu kwa m’bale wanu Adoniya kuti akhale mkazi wake.” 22 Mfumu Solomo itamva zimenezi inafunsa mayi ake kuti: “N’chifukwa chiyani mukum’pemphera Adoniyayu Abisagi Msunemu? M’pemphereninso ufumu+ (chifukwa iye ndi mkulu wanga).+ Mupemphereni ufumu Adoniyayo. Mupempherenso wansembe Abiyatara+ ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya.”+

23 Mfumu Solomo itatero, inalumbira pamaso pa Yehova kuti: “Mulungu andilange mowirikiza+ ngati Adoniya sanaike moyo wake pangozi mwa kupempha zimenezi.+ 24 Tsopano m’dzina la Yehova Mulungu wamoyo,+ amene wandichititsa kukhazikika,+ amene wandiika pampando wachifumu wa Davide bambo anga,+ ndiponso amene anandipatsa mzere wa banja lachifumu+ monga ananenera,+ lero Adoniya aphedwa.”+ 25 Nthawi yomweyo Mfumu Solomo inatumiza lamulo kudzera mwa Benaya+ mwana wa Yehoyada. Iye anapita kukakantha Adoniya, n’kumupha.+

26 Kwa wansembe Abiyatara,+ mfumuyo inati: “Pita kuminda yako ku Anatoti+ chifukwa ukuyenera kufa.+ Koma lero sindikupha, poti unanyamula likasa la Yehova Ambuye Wamkulu Koposa+ pamaso pa Davide bambo anga,+ ndiponso chifukwa chakuti unavutika nthawi yonse imene bambo anga anavutika.”+ 27 Choncho Solomo anathamangitsa Abiyatara n’kumusiyitsa kutumikira monga wansembe wa Yehova, pokwaniritsa mawu amene Yehova analankhula ku Silo,+ otsutsana ndi nyumba ya Eli.+

28 Nkhaniyo inam’fika Yowabu,+ ndipo iye anathawira kuchihema+ cha Yehova n’kukagwira nyanga za guwa lansembe.+ Paja Yowabu ankatsatira Adoniya,+ ngakhale kuti sanatsatire+ Abisalomu. 29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova, ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, kuti: “Pita ukamuphe!”+ 30 Benaya anapitadi kuchihema cha Yehova n’kukamuuza Yowabu kuti: “Mfumu yanena kuti, ‘Tuluka!’” Koma iye anati: “Ayi! Ndifera mom’muno.”+ Benaya atamva zimenezo anakauza mfumu kuti: “Yowabu wanena zimenezi, ndipo wandiyankha choncho.” 31 Mfumuyo inamuuza kuti: “Chita zimene wakuuzazo. Umuphe n’kumuika m’manda ndi kundichotsera ine ndi nyumba ya bambo anga magazi+ amene Yowabu anakhetsa+ popanda chifukwa. 32 Ukatero, Yehova adzabwezeradi pamutu pake magazi ake,+ chifukwa anakantha amuna awiri olungama ndi abwino kuposa iyeyo,+ ndipo anawapha ndi lupanga. Anachita zimenezi Davide bambo anga osadziwa.+ Amuna ake anali Abineri+ mwana wa Nera mkulu wa asilikali a Isiraeli,+ ndi Amasa+ mwana wa Yeteri mkulu wa asilikali a Yuda.+ 33 Magazi awo ayenera kubwerera pamutu pa Yowabu ndi pamutu pa mbumba yake mpaka kalekale.+ Koma kwa Davide,+ mbumba yake, nyumba yake, ndi mpando wake wachifumu, kudzakhala mtendere wochokera kwa Yehova mpaka kalekale.”+ 34 Kenako Benaya mwana wa Yehoyada anapita+ kuchihemako n’kukakantha Yowabu ndi kumupha,+ ndipo anaikidwa m’manda panyumba pake m’chipululu. 35 Zitatero, mfumu inaika Benaya+ mwana wa Yehoyada m’malo mwa Yowabu kuti akhale mkulu wa asilikali,+ ndipo inaika wansembe Zadoki m’malo mwa Abiyatara.+

36 Pomaliza mfumu inatuma anthu kukaitana Simeyi,+ ndipo inamuuza kuti: “Udzimangire nyumba ku Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko. Usachoke kumeneko kupita kwina ndi kwina. 37 Zikadzachitika kuti tsiku lina wachoka n’kudutsa chigwa* cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa ndithu.+ Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.”+ 38 Simeyi atamva zimenezi anauza mfumu kuti: “Mwanena bwino. Mmene mbuyanga mfumu mwanenera, ndi mmenenso mtumiki wanu achitire.” Ndipo Simeyi anakhala ku Yerusalemu masiku ambiri.

39 Pamapeto pa zaka zitatu, akapolo awiri+ a Simeyi anathawira kwa Akisi+ mwana wa Maaka, mfumu ya Gati.+ Kenako anthu anabwera kudzauza Simeyi kuti: “Tamvera! Akapolo ako ali ku Gati.” 40 Nthawi yomweyo, Simeyi anaimirira n’kukwera bulu wake kupita ku Gati kwa Akisi, kukafunafuna akapolo akewo. Choncho Simeyi anapita ku Gati n’kukabwerako ndi akapolo ake. 41 Ndiyeno Solomo anauzidwa kuti: “Simeyi anatuluka mu Yerusalemu kupita ku Gati, ndipo wabwerako.” 42 Mfumuyo itamva inatuma anthu kukaitana+ Simeyi. Atafika, inam’funsa kuti: “Kodi sindinakulumbiritse pamaso pa Yehova n’kukuchenjeza+ kuti, ‘Tsiku limene udzatuluke kunja n’kupita kwina ndi kwina, udziwiretu kuti udzafa ndithu’? Ndipo kodi iwe sunandiuze kuti, ‘Mawu mwanenawa ndi abwino’?+ 43 Nangano n’chifukwa chiyani sunasunge lumbiro limene unapanga pamaso pa Yehova,+ ndi lamulo limene ndinakulamula mwamphamvu?”+ 44 Ndiyeno mfumuyo inapitiriza kuuza Simeyi kuti: “Iweyo wekha ukudziwa bwino mumtima mwako zoipa zonse zimene unachitira Davide bambo anga.+ Yehova akubwezera ndithu pamutu pako zoipa zimene unachita.+ 45 Koma Mfumu Solomo idzadalitsidwa,+ ndipo mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika kwamuyaya pamaso pa Yehova.”+ 46 Itatero, mfumuyo inalamula Benaya mwana wa Yehoyada amene ananyamuka n’kukakantha Simeyi, ndipo anafa.+

Choncho ufumuwo unakhazikika m’manja mwa Solomo.+

3 Kenako Solomo anachita mgwirizano wa ukwati+ ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anatenga mwana wamkazi wa Faraoyo+ n’kubwera naye ku Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova,+ ndi mpanda wozungulira Yerusalemu yense.+ 2 Anthuwo anali kupereka nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa anali asanamange nyumba ya dzina la Yehova mpaka masiku amenewo.+ 3 Solomo anapitiriza kukonda+ Yehova mwa kuyenda motsatira malamulo a Davide bambo ake,+ kungoti nthawi zonse anali kupereka nsembe zopsereza pamalo okwezeka.+

4 Chotero mfumu inapita ku Gibeoni+ kukapereka nsembe, chifukwa kumeneko ndiye kunali malo okwezeka ofunika kwambiri.+ Kumeneko, Solomo anapereka nsembe zopsereza zokwana 1,000 paguwa lansembe.+ 5 Ku Gibeoniko, Yehova Mulungu anaonekera+ kwa Solomo m’maloto+ usiku ndipo anati: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.”+ 6 Solomo atamva anati: “Inu mwasonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa mtumiki wanu Davide bambo anga, popeza anayenda pamaso panu m’choonadi ndi m’chilungamo+ ndiponso anali wowongoka mtima pamaso panu. Munapitiriza kumusonyeza kukoma mtima kosatha kumeneku moti munam’patsa mwana kuti lero akhale pampando wake wachifumu.+ 7 Tsopano Yehova Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune kukhala mfumu m’malo mwa Davide bambo anga. Komatu ndine mwana+ ndipo sindikudziwa zinthu zambiri.+ 8 Mtumiki wanune ndili pakati pa anthu anu amene mwawasankha,+ anthu ochuluka zedi amene sangatheke kuwerengeka chifukwa chochuluka.+ 9 Mupatse mtumiki wanune mtima womvera kuti ndiweruze+ anthu anu, ndi kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa,+ pakuti ndani angathe kuweruza+ anthu anu ovutawa?”+

10 Zimene anapempha Solomozi zinamusangalatsa Yehova.+ 11 Ndiyeno Mulungu anamuuza kuti: “Popeza wapempha zimenezi ndipo sunapemphe masiku ambiri, chuma,+ kapena moyo wa adani ako, koma wapempha kuti ukhale womvetsa zinthu kuti uzitha kuweruza milandu,+ 12 taona, ndichita mogwirizanadi ndi mawu ako.+ Ndithu ndikupatsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu+ moti ndi kale lonse sipanakhalepo munthu ngati iwe, ndipo pambuyo pako sipadzakhalanso wina ngati iwe.+ 13 Ndikupatsanso zomwe sunapemphe,+ chuma+ ndi ulemerero, moti sikudzakhalanso mfumu ngati iwe masiku ako onse.+ 14 Ndipo ukayenda m’njira zanga mwa kusunga malangizo ndi malamulo anga+ monga momwe Davide bambo ako anayendera,+ ndidzatalikitsanso masiku ako.”+

15 Solomo atagalamuka,+ anazindikira kuti waona masomphenya. Kenako anapita ku Yerusalemu n’kukaimirira pamaso pa likasa+ la pangano la Yehova. Ndiyeno anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano+ n’kukonzera phwando+ atumiki ake onse.+

16 Kenako akazi awiri omwe anali mahule+ anapita kwa mfumu n’kuima pamaso pake.+ 17 Mmodzi wa akaziwo anati: “Pepani mbuyanga,+ ine ndi mayi uyu tikukhala m’nyumba imodzi. Ineyo ndinabereka mwana wamwamuna pafupi naye m’nyumbamo. 18 Patapita masiku atatu kuchokera tsiku limene ine ndinabereka mwana, mayi uyu nayenso anabereka mwana wamwamuna. Ndipo tinali limodzi. M’nyumbamo munalibe munthu wina aliyense kupatulapo awirife. 19 Kenako mwana wa mayiyu anafa usiku chifukwa anam’tsamira. 20 Choncho kapolo wanune ndili m’tulo, mayiyu anadzuka pakati pa usiku n’kutenga mwana wanga amene anali pambali panga, n’kumuika pachifuwa pake. Ndiyeno anatenga mwana wake wakufayo n’kumuika pachifuwa panga. 21 Nditadzuka kuti ndiyamwitse+ mwana wanga, ndinapeza kuti anali wakufa. Choncho ndinamuyang’anitsitsa kwambiri m’mawa n’kuona kuti si mwana wanga amene ndinabereka.” 22 Koma mayi wina uja anati: “Ayi, mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!” Ndipo mayi woyamba uja anali kunena kuti: “Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu.” Iwo anapitiriza kulankhula choncho pamaso pa mfumu.+

23 Pomaliza mfumuyo inati: “Uyu akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!’ Ndipo uyo akuti, ‘Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu!’” 24 Ndiyeno mfumuyo inati:+ “Amuna inu, ndibweretsereni lupanga.” Choncho anabweretsa lupanga pamaso pa mfumu. 25 Mfumuyo inati: “Amuna inu, dulani mwana wamoyoyu pakati. Mupereke hafu ya mwanayo kwa mayi mmodzi ndi hafu inayo kwa mayi winayo.” 26 Popeza mtima wa mayi yemwe mwana wake anali wamoyoyo unayamba kugunda kwambiri+ chifukwa cha mwana wakeyo,+ nthawi yomweyo anauza mfumuyo kuti: “Pepani+ mbuyanga! Amuna inu, m’patseni mayiyu mwana wamoyoyu. Musamuphe ayi.” Apa n’kuti mayi wina uja akunena kuti: “Mwanayu sakhala wanga kapena wako. Amuna inu, m’duleni!”+ 27 Mfumuyo itamva zimenezi inati: “Amuna inu, perekani mwana wamoyoyu kwa mayi uyu. Musamuphe ayi. Ameneyu ndiye mayi wake.”

28 Aisiraeli onse anamva za chigamulo+ chimene mfumu inapereka, ndipo anachita mantha chifukwa cha mfumuyo,+ popeza anaona kuti nzeru+ za Mulungu zinali mwa iye kuti azipereka zigamulo.

4 Mfumu Solomo inapitiriza kulamulira Isiraeli yense.+ 2 Ndipo awa ndiwo akalonga+ amene inali nawo: Wansembe Azariya mwana wa Zadoki,+ 3 Elihorefi ndi Ahiya, ana a Sisa, omwe anali alembi,+ ndi wolemba zochitika dzina lake Yehosafati,+ mwana wa Ahiludi. 4 Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mkulu wa asilikali,+ ndipo Zadoki ndi Abiyatara+ anali ansembe. 5 Azariya mwana wa Natani+ anali mkulu wa nduna, ndipo Zabudu mwana wa Natani anali wansembe, bwenzi+ la mfumu. 6 Ahisara anali woyang’anira banja lachifumu, ndipo Adoniramu,+ mwana wa Abada, anali woyang’anira anthu olembedwa ntchito yokakamiza.+

7 Solomo anali ndi nduna 12 mu Isiraeli yense, zomwe zinkabweretsa chakudya kwa mfumu ndi banja lake lachifumu. Nduna iliyonse inali ndi udindo wobweretsa chakudya kwa mwezi umodzi pachaka.+ 8 Mayina a ndunazo anali awa: Mwana wa Hura, kudera lamapiri la Efuraimu,+ 9 mwana wa Dekeri, amene ankayang’anira ku Makazi, ku Saalibimu,+ ku Beti-semesi,+ ndi ku Eloni-beti-hanani, 10 mwana wa Hesedi, ku Aruboti (dera lake linali Soko ndi dera lonse la Heferi),+ 11 mwana wa Abinadabu, kumapiri onse a Dori+ (Tafati mwana wa Solomo anadzakhala mkazi wake), 12 Baana mwana wa Ahiludi, ku Taanaki+ ndi ku Megido+ ndi ku Beti-seani+ konse, pafupi ndi Zeretani+ kumunsi kwa Yezereeli,+ kuchokera ku Beti-seani kukafika ku Abele-mehola+ mpaka kuchigawo cha Yokimeamu,+ 13 mwana wa Geberi ku Ramoti-giliyadi+ (dera lake linali midzi ing’onoing’ono ya Yairi+ mwana wa Manase, yomwe ili ku Giliyadi.+ Analinso ndi chigawo cha Arigobi,+ chomwe chili ku Basana.+ Kunali mizinda ikuluikulu 60 yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso mipiringidzo yamkuwa), 14 Ahinadabu mwana wa Ido, ku Mahanaimu,+ 15 Ahimazi ku Nafitali+ (nayenso anakwatira mwana wa Solomo, Basemati),+ 16 Baana mwana wa Husai, ku Aseri+ ndi ku Bealoti, 17 Yehosafati mwana wa Paruwa, ku Isakara,+ 18 Simeyi+ mwana wa Ela, ku Benjamini,+ 19 Geberi mwana wa Uri, ku Giliyadi,+ m’dera la Sihoni+ mfumu ya Aamori,+ ndi la Ogi+ mfumu ya Basana.+ Panalinso nduna imodzi yoyang’anira nduna zonse m’dzikomo.

20 Ayuda ndi Aisiraeli anachuluka kwambiri.+ Kuchuluka kwake anali ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja, ndipo anali kudya, kumwa, ndi kusangalala.+

21 Solomo anakhala wolamulira wa maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumu amenewa anali kubweretsa mphatso kwa Solomo ndi kum’tumikira masiku onse a moyo wake.+

22 Chakudya cha kunyumba yachifumu ya Solomo tsiku lililonse chinkakhala ufa wosalala wokwana miyezo 30 ya kori,*+ ufa wamba wokwana miyezo 60 ya kori, 23 ng’ombe 10 zodyetsera m’khola, ng’ombe 20 zodyetsera kutchire, nkhosa 100, ndiponso mbawala zamphongo,+ insa,+ ngondo, ndi mbalame zoweta zonona. 24 Iye ankalamulira chilichonse kumbali yakuno ya Mtsinje,+ kuchokera ku Tifisa mpaka ku Gaza.+ Ankalamulira mafumu onse a mbali yakuno ya Mtsinje,+ ndipo m’zigawo zake zonse munali mtendere.+ 25 Ayuda+ ndi Aisiraeli anapitiriza kukhala mwabata.+ Aliyense anali pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+ kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ masiku onse a Solomo.

26 Solomo anali ndi makola 40,000 a mahatchi+ okoka magaleta ake,+ ndi amuna 12,000 okwera pamahatchi.

27 Nduna+ zinkabweretsa chakudya cha Mfumu Solomo ndi cha aliyense wodyera limodzi ndi mfumuyo. Nduna iliyonse inkabweretsa chakudya kwa mwezi umodzi, ndipo inkaonetsetsa kuti pasakhale choperewera. 28 Ankabweretsanso balere ndi chakudya cha mahatchi okoka magaleta ndiponso cha mahatchi ena.+ Ankachipititsa kulikonse komwe chikufunika, aliyense malinga ndi udindo wake.+

29 Mulungu anapitiriza kupatsa Solomo nzeru zopanda malire ndi luso lomvetsa zinthu losaneneka.+ Anam’patsanso mtima wozindikira zinthu mwakuya.+ 30 Nzeru za Solomo zinaposa+ nzeru za anthu onse a Kum’mawa+ ndi nzeru zonse za ku Iguputo.+ 31 Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense. Anali wanzeru kuposa Etani+ mwana wa Zera, Hemani,+ Kalikoli,+ ndi Darida ana a Maholi. Ndipo anatchuka m’mitundu yonse yozungulira.+ 32 Ankalankhula miyambi 3,000+ ndipo nyimbo zake+ zinakwana 1,005. 33 Ankafotokoza za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni+ mpaka kamtengo ka hisope+ kamene kamamera pakhoma.* Ankafotokozanso za zinyama,+ zolengedwa zouluka,+ nsomba,+ ndiponso za zokwawa.+ 34 Ndipo anthu ankabwera kuchokera ku mitundu yonse kudzamva nzeru za Solomo,+ ngakhalenso kuchokera kwa mafumu onse a padziko lapansi amene anamva za nzeru zake.+

5 Hiramu+ mfumu ya ku Turo+ inatumiza atumiki+ ake kwa Solomo, pakuti inamva kuti iyeyo ndi amene anadzozedwa kulowa ufumu m’malo mwa bambo ake, popeza Hiramuyo ankamukonda Davide masiku ake onse.+ 2 Kenako Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu, kuti:+ 3 “Inuyo mukudziwa bwino kuti Davide bambo anga sanathe kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo+ zimene adani ake ankamenyana naye m’madera onse omuzungulira, mpaka pamene Yehova anaika adani akewo pansi pa mapazi ake. 4 Tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mpumulo pakati pa adani anga onse ondizungulira.+ Palibe amene akulimbana nane, ndipo palibe choipa chilichonse chimene chikuchitika.+ 5 Panopa ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga,+ monga momwe Yehova analonjezera Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu m’malo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 6 Tsopano lamulani kuti anthu andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga adzakhala limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzakupatsani malipiro a antchito anu malingana ndi zonse zomwe munganene. Inuyo mukudziwa bwino kuti pakati pathu palibenso anthu odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+

7 Hiramu+ atangomva mawu a Solomo, anasangalala kwambiri ndipo ananena kuti: “Yehova atamandike+ lero, popeza wapereka kwa Davide mwana wanzeru+ woti alamulire anthu ochulukawa.”+ 8 Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo, kuti: “Ndamva uthenga wanu. Ineyo ndichita zonse zimene mukufuna pa nkhani ya mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza.+ 9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni+ n’kutsikira nayo kunyanja, ndipo ineyo kumbali yanga ndidzaimanga pamodzi ngati phaka n’kuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze.+ Kenako ndidzauza anthu kuti aimasule, ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Ndipo inu mudzachita zofuna zanga pondipatsa chakudya cha banja langa.”+

10 Choncho Hiramu anapereka kwa Solomo mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza, monga momwe Solomo anafunira. 11 Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori,*+ kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta oyenga bwino kwambiri+ okwana miyezo 20 ya kori. Izi n’zimene Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka ndi chaka.+ 12 Ndiyeno Yehova anapatsa Solomo nzeru monga mmene anam’lonjezera.+ Pakati pa Hiramu ndi Solomo panali mtendere, ndipo awiriwa anachita pangano.

13 Anthu amene Mfumu Solomo inawalemba ntchito yokakamiza anachokera ku Isiraeli konse, ndipo anthu olembedwa ntchito yokakamizawo+ anakwana amuna 30,000. 14 Inkawatumiza ku Lebanoni m’magulu a anthu 10,000 pamwezi. Kwa mwezi umodzi anthuwo ankakhala ku Lebanoni, ndipo kwa miyezi iwiri ankakhala kwawo.+ Adoniramu+ ndiye anali woyang’anira anthu olembedwa ntchito yokakamizawo.+ 15 Solomo anali ndi anthu+ 70,000 onyamula katundu,+ ndi ena 80,000 osema miyala+ kumapiri.+ 16 Kuwonjezera pa amenewa, panalinso akapitawo a nduna za Solomo+ oyang’anira ntchitoyo. Analipo akapitawo 3,300+ oyang’anira anthu amene anali kugwira ntchitoyo. 17 Ndiyeno mfumuyo inalamula kuti aseme miyala ikuluikulu yokwera mtengo,+ kuti akamange maziko+ a nyumbayo ndi miyala yosema.+ 18 Choncho amisiri omanga a Solomo ndi amisiri omanga a Hiramu ndiponso Agebala+ anasema miyalayo, ndipo anapitiriza kudula mitengo ndi kusema miyala pokonzekera kumanga nyumbayo.

6 Tsopano Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova.+ Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ m’mwezi wachiwiri+ wa Zivi.+ Ichi chinali chaka chachinayi+ cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli. 2 Nyumba imene Mfumu Solomo inamangira+ Yehova, m’litali mwake inali mikono* 60,+ m’lifupi mwake inali mikono 20, ndipo kutalika kwake inali mikono 30.+ 3 Khonde+ la kutsogolo kwa chipinda chachikulu* cha nyumbayo linali mikono 20 m’litali, kufanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Khondelo linali kutsogolo kwa nyumbayo, ndipo linali mikono 10 m’lifupi mwake.

4 Nyumbayo anaiika mawindo. Mawindo ake anali aakulu mkati, aang’ono kunja.+ 5 Komanso, anamanga zipinda kuzungulira khoma lonse la nyumbayo, kuzungulira makoma onse akunja a chipinda chachikulu ndi chipinda chamkati.+ Anamanga zipinda zam’mbali+ zosanjikizana kuzungulira nyumba yonseyo. 6 Chipinda cham’mbali chapansi chinali mikono isanu m’lifupi mwake. Chipinda cham’mbali chapakati chinali mikono 6 m’lifupi mwake, ndipo chipinda cham’mbali chachitatu chinali mikono 7 m’lifupi mwake. Makoma onse akunja a nyumbayo anangowagoba+ n’cholinga choti asawaboole.+

7 Nyumbayo anaimanga ndi miyala yosema+ kale, ndipo kulira kwa nyundo, nkhwangwa, kapena zida zilizonse zachitsulo sikunamveke m’nyumbayo+ pamene anali kuimanga. 8 Khomo lolowera+ kuchipinda cham’mbali chapansi linali kumanja kwa nyumbayo, ndipo ankakwera masitepe oyenda chokhotakhota kukafika kuchipinda chapakati. Kuchokera kuchipinda chimenechi, ankakwera n’kukafika kuchipinda chachitatu. 9 Anapitiriza kumanga nyumbayo kuti aimalize,+ ndipo mkati mwa nyumbayo anamangamo ndi matabwa ndi mitanda ya mitengo ya mkungudza.+ 10 Anamanga zipinda zam’mbali+ zosanjikizana kuzungulira nyumba yonseyo. Chipinda chilichonse chinali chotalika mikono isanu. Zipindazo anazilumikiza kunyumbayo ndi matabwa+ a mkungudza.

11 Pa nthawiyo, Yehova anauza Solomo+ kuti:+ 12 “Kunena za nyumba ukumangayi, ukayenda motsatira malamulo+ anga ndi kusunga zigamulo+ zanga zonse ndi kuzitsatira,+ inenso ndidzakwaniritsadi mawu anga okhudza iweyo amene ndinalankhula kwa bambo ako Davide.+ 13 Ndidzakhaladi pakati pa ana a Isiraeli,+ ndipo sindidzasiya anthu anga, Aisiraeli.”+

14 Solomo anapitiriza kumanga nyumbayo kuti aimalize.+ 15 Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga* anakutamo ndi matabwa. Kenako anakuta pansi pa nyumbayo ndi matabwa akuluakulu a mitengo yofanana ndi mkungudza.+ 16 Komanso, anagawa chigawo cha mikono 20 kumbuyo kwa nyumbayo ndi matabwa a mkungudza, kuchokera pansi mpaka kudenga. Nyumbayo anaimangira chipinda chamkati,+ chotchedwa Malo Oyera Koposa.+ 17 Chipinda chachikulu kutsogolo+ kwa nyumbayo+ chinali mikono 40. 18 Pamatabwa a mkungudza a mkati mwa nyumbayo anajambulapo mochita kugoba zokongoletsera zooneka ngati zipanda+ ndi nkhata zamaluwa.+ Mkati monse munali matabwa a mkungudza ndipo simunkaoneka mwala uliwonse.

19 Iye anakonza mkati mwa chipinda chamkati+ cha nyumbayo kuti aikemo likasa+ la pangano+ la Yehova. 20 Chipinda chamkati chinali mikono 20 m’litali, mikono 20 m’lifupi+ ndi mikono 20 kutalika kwake. Chipindacho anachikuta ndi golide woyenga bwino,+ komanso anakuta guwa lansembe+ ndi matabwa a mkungudza. 21 Solomo anakuta+ mkati mwa nyumba yonseyo ndi golide woyenga bwino.+ Anatenga matcheni+ agolide ndi kuwadutsitsa kutsogolo kwa chipinda chamkati,+ n’kukuta chipindacho ndi golide. 22 Nyumba yonseyo anaikuta ndi golide+ mpaka kuimaliza, ndipo guwa lansembe lonse,+ lomwe linali kufupi ndi chipinda chamkati, analikuta ndi golide.+

23 Komanso, m’chipinda chamkati anapangamo akerubi+ awiri kuchokera ku mtengo wamafuta.* Kerubi aliyense anali mikono 10 kutalika kwake.+ 24 Phiko limodzi la kerubi linali lalitali mikono isanu, ndipo phiko linalo linali lalitali mikono isanunso. Kuchokera kunsonga ya phiko lake limodzi kufika kunsonga ya phiko lake lina, kutalika kwake kunali kukwana mikono 10.+ 25 Kerubi wachiwiri anali wotalika mikono 10. Akerubi awiriwo anali ofanana kukula kwawo ndiponso kapangidwe kawo. 26 Kerubi mmodzi anali mikono 10 kutalika kwake, ndipo winayonso anali chimodzimodzi. 27 Kenako anaika akerubiwo m’chipinda chamkati, ndipo mapiko awo anali otambasula.+ Nsonga ya phiko la kerubi mmodzi inagunda khoma ndipo nsonga ya phiko la kerubi winayo inagundanso khoma lina. Mapiko awo anafika pakati pa nyumbayo, ndipo anagundana.+ 28 Kenako Solomo anakuta akerubiwo ndi golide.+

29 Pamakoma onse a nyumbayo, m’zipinda zonse ziwiri, chamkati ndi chakunja, anajambulapo akerubi,+ mitengo ya kanjedza,+ ndi maluwa.+ Anajambula zinthu zimenezi mochita kugoba. 30 Pansi+ pa nyumbayo, m’zipinda zonse ziwiri, chamkati ndi chakunja, anakutapo ndi golide. 31 Pakhomo la chipinda chamkati anaikapo zitseko+ za mtengo wamafuta,+ zipilala za m’mbali, ndi mafelemu. Zimenezi zinali mbali yachisanu. 32 Zitseko ziwirizo zinali za matabwa a mtengo wa mafuta. Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza, ndi maluwa, ndipo anazikuta ndi golide. Kenako akerubi ndi mitengo ya kanjedza yolemba mochita kugoba ya pazitsekozo, anazikuta ndi golide. 33 Anapanganso zomwezo pakhomo la chipinda chachikulu, pamafelemu ake a mtengo wamafuta omwe anali ofanana mbali zonse kutalika kwake. 34 Zitseko ziwirizo zinali za matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza.+ Zitseko ziwiri za khomo limodzi zinkayenda pamiyendo yake, ndipo zitseko ziwiri za khomo linalo zinkayendanso pamiyendo yake.+ 35 Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza, ndi maluwa ndipo anakuta zojambulazo ndi golide.+

36 Kenako anamanga khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu+ kuzungulira bwalo lamkati,+ ndipo anawonjezeranso mzere umodzi wa matabwa a mkungudza.

37 M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomo, m’mwezi wa Zivi,+ anamanga maziko+ a nyumba ya Yehova. 38 Ndipo m’chaka cha 11, m’mwezi wa Buli,* womwe ndi mwezi wa 8, anamaliza+ kumanga zinthu zonse panyumbayo motsatira mapulani ake onse.+ Motero, Solomo anatha zaka 7 akumanga nyumbayo.

7 Solomo anatha zaka 13+ akumanga nyumba yake, ndipo anaimanga n’kuimaliza yonse.+

2 Kenako anamanga nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ Nyumbayi inali mikono 100 m’litali, mikono 50 m’lifupi, ndi mikono 30 kutalika kwake. Anaimanga pamwamba pa nsanamira za mtengo wa mkungudza. Nsanamirazo zinali m’mizere yokwanira inayi. Pamwamba pa nsanamirazo+ panali mitengo ya mkungudza yodutsa chopingasa. 3 Nyumba imeneyi anaimanga ndi matabwa a mkungudza+ kuyambira pazitsulo zimene zinali pamwamba pa nsanamira kupita m’mwamba. Nsanamirazo zinalipo 45, ndipo pamzere uliwonse panali nsanamira* 15. 4 Nyumbayi inali yosanja kawiri. Nsanjika iliyonse inali ndi mzere wa mawindo. Chotero nyumba yonseyo inali ndi mizere itatu ya mawindo okhala ndi mafelemu. Mawindowo+ anayang’anizana ndi mawindo a mbali ina ya nyumbayo. 5 Makomo onse a nyumbayo anali ndi mafelemu okhala ndi mbali zonse zinayi zofanana.+ Mbali ya mkati ya windo loyang’anizana ndi windo lina inali ndi felemu lokhala ndi mbali zinayi zofanana. Zinali chonchi mu nsanjika zonse zitatu za nyumbayi.

6 Kenako anamanga Khonde la Zipilala. M’litali mwake linali mikono 50, ndipo m’lifupi mwake linali mikono 30. Kutsogolo kwa zipilalazo kunali khonde lina lokhalanso ndi zipilala ndi denga.

7 Anamanganso Bwalo la Mpando Wachifumu,+ kumene anali kuweruzirako milandu. Bwaloli linkatchedwanso bwalo loweruzira.+ Makoma ake anali a matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka kudenga.+

8 Kenako Solomo anamanga nyumba yake yokhalamo kubwalo lina+ chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka Bwalo la Mpando Wachifumu. Panalinso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli imene Solomo anamangira mwana wamkazi wa Farao+ amene iye anam’kwatira.

9 Nyumba zonsezi, kuyambira pamaziko ake mpaka pamwamba pa khoma, ndiponso kuchokera panja pa nyumbazo mpaka kubwalo lalikulu,+ zinamangidwa ndi miyala yokwera mtengo+ yochita kuyeza, ndiponso yocheka ndi macheka a miyala, mkati ndi kunja komwe. 10 Miyala yokwera mtengo imene anamangira maziko inali ikuluikulu. Kukula kwake ina inali mikono 10, ina mikono 8. 11 Pamwamba pa miyala ya mazikoyo panalinso miyala ina yokwera mtengo yochita kuyeza ndiponso yosema. Anagwiritsiranso ntchito matabwa a mkungudza. 12 Kuzungulira bwalo lalikulu panali khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu+ kuchokera pansi, ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza pamwamba pake. Bwalo lamkati+ la nyumba+ ya Yehova ndi khonde+ la nyumbayo, zinamangidwanso mofanana.

13 Kenako Mfumu Solomo inatuma anthu kuti akatenge Hiramu+ ku Turo. 14 Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo+ odziwa kupanga zinthu ndi mkuwa.+ Hiramu anali wanzeru, womvetsa bwino zinthu,+ ndiponso wodziwa bwino kupanga zinthu zosiyanasiyana zamkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo n’kuyamba kumugwirira ntchito yake yonse.

15 Anaumba zipilala ziwiri zamkuwa.+ Kutalika kwa chipilala chilichonse kunali mikono 18, ndipo pankafunika chingwe chotalika mikono 12 kuti ayeze kuzungulira chipilala chilichonse.+ 16 Anapanga mitu iwiri youmba ndi mkuwa+ n’kuiika pamwamba pa zipilalazo. Mutu umodzi kutalika kwake kunali mikono isanu, ndipo mutu winawo kutalika kwake kunalinso mikono isanu. 17 Anapanga maukonde olukanalukana ndiponso zokongoletsera zolukanalukana ngati tcheni,+ za mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo.+ Anapanga zimenezi zokwanira 7 za mutu umodzi, ndi zinanso 7 za mutu winawo. 18 Kenako anapanga mizere iwiri ya makangaza* n’kuwazunguliza pamaukonde awiri aja, n’kuveka mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo. Anachita zimenezi pamitu+ yonse iwiri. 19 Mitu imene inali pamwamba pa zipilala, pafupi ndi khonde, anaipanga ngati maluwa+ ndipo kutalika kwake inali mikono inayi. 20 Mitu iwiriyo inali pamwamba pa zipilala, komanso inali pamwamba pa mimba imene inagundana ndi maukonde. Kuzungulira mutu uliwonse, panali makangaza 200+ amene anali m’mizere.

21 Ndiyeno Hiramu anaika zipilala+ zija pakhonde+ la kachisi. Chipilala chimodzi anachiika mbali ya kudzanja lamanja n’kuchitcha Yakini. Chipilala china anachiika mbali ya kumanzere n’kuchitcha Boazi. 22 Pamwamba pa chipilala chilichonse panali pooneka ngati duwa. M’kupita kwa nthawi, ntchito yoika zipilalazo inatha.

23 Kenako iye anapanga thanki yamkuwa.*+ Pakamwa pa thankiyo panali papakulu mikono 10 kuyeza modutsa pakati pake, ndipo panali pozungulira. Thankiyo inali yaitali mikono isanu kuchokera pansi kufika pamwamba. Pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira thankiyo.+ 24 Kuzungulira m’khosi mwake monse munali zokongoletsera+ zooneka ngati zipanda.+ Zinalipo 10 pa mkono uliwonse kuzungulira thanki yonseyo.+ Zokongoletsa zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 25 Thankiyo anaikhazika pang’ombe zamphongo 12.+ Ng’ombe zitatu zinayang’ana kumpoto, zitatu zinayang’ana kumadzulo, zitatu zinayang’ana kum’mwera, ndipo zitatu zinayang’ana kum’mawa. Thankiyo inali pamwamba pa ng’ombezo ndipo mbuyo zonse za ng’ombezo zinaloza pakati.+ 26 Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi.+ Mlomo wake unali ngati wa mphika wakukamwa ngati duwa.+ M’thankiyo munkalowa+ madzi okwana mitsuko* 2,000.+

27 Kenako anapanga zotengera 10+ zamkuwa zokhala ndi mawilo. Chotengera chilichonse chinali mikono inayi m’litali, mikono inayi m’lifupi, ndi mikono itatu kutalika kwake kuchokera pansi kukafika pamwamba. 28 Zotengerazo zinapangidwa motere: Zinali ndi malata m’mbali mwake, ndipo malatawo anali pakati pa zitsulo zopingasana. 29 Pamalata amene anali pakati pa zitsulo zopingasana anajambulapo mikango,+ ng’ombe zamphongo,+ ndi akerubi.+ Pazitsulo zopingasana anajambulaponso zimenezo mochita kugoba. Pamwamba ndi pansi pa mikango ndi ng’ombe zamphongozo, anajambulapo mochita kugoba nkhata zamaluwa+ zopendeketsa. 30 Chotengera chilichonse chinali ndi mawilo anayi amkuwa ndi mitanda yamkuwa yolumikiza wilo ndi wilo linzake. M’makona ake anayi munali zogwiriziza mawilo, ndipo zogwirizizazo zinkafika pansi pa beseni. Zogwirizizazo anazipangira kumodzi ndi nkhata zamaluwa zochokera pa chogwiriziza chilichonse. 31 Pakamwa pake, kuyambira mkati n’kukwera m’mwamba kuchokera pa zogwiriziza, inali mikono [?].* Kamwa lake linali lozungulira lopangidwa kuti azikhazikapo beseni. Kutalika kwa kamwalo kunali mkono umodzi ndi hafu. Pakamwapo anajambulapo zinthu zokongoletsera. Zinthuzo anazijambula mochita kugoba. Malata a m’mbali mwake anali a mbali zinayi zofanana, osati ozungulira. 32 Pansi pa malata a m’mbaliwo panali mawilo anayi. Zogwiriziza za mawilowo zinali m’makona a chotengeracho. Wilo lililonse linali mkono umodzi ndi hafu kutalika kwake. 33 Mawilowo anawapanga ngati mawilo a galeta.+ Zogwiriziza zake, zingelengele zake, masipokosi ake, ndi mahabu ake, zonse zinali zoumba ndi mkuwa. 34 Panali zogwiriziza zinayi, chimodzi pa kona iliyonse ya chotengera. Chotengera chilichonse chinali ndi makona anayi. Zogwiriziza zake anaziumbira kumodzi ndi chotengeracho. 35 Pamwamba pa chotengeracho panali chokhazikapo beseni. Chokhazikapo besenicho chinali chozungulira, ndipo kutalika kwake kunali hafu ya mkono kuchokera pansi kufika pamwamba. Chokhazikapo besenicho anachipangira kumodzi ndi chotengeracho ndiponso ndi malata ake a m’mbali. 36 Komanso pamalata a m’mbali mwa chokhazikapo besenicho, ndi pazitsulo zimene zinali pakati pa malatawo, anajambulapo mochita kugoba+ akerubi, mikango, ndi mitengo yakanjedza malinga ndi kukula kwa malo ake. Anajambulanso mochita kugoba nkhata zamaluwa kuzungulira chokhazikapo besenicho.+ 37 Mmenemu ndi mmene zotengera 10+ zimenezo anazipangira. Zinali zoumbidwa chimodzimodzi,+ kukula kwake chimodzimodzi, ndiponso zooneka chimodzimodzi.

38 Kenako anapanga mabeseni 10+ amkuwa. Beseni lililonse linali lokwana mitsuko* 40, ndipo linali mikono inayi kukula kwake. Pachotengera chilichonse mwa zotengera 10 zija panali beseni limodzi. 39 Anaika zotengera zisanu mbali ya kudzanja lamanja kwa nyumbayo ndi zotengera zina zisanu mbali ya kumanzere kwa nyumbayo.+ Thanki ija anaiika mbali ya kudzanja lamanja kwa nyumbayo, kum’mawa chakum’mwera kwake.+

40 M’kupita kwa nthawi Hiramu+ anapanga mabeseni,+ mafosholo+ ndi mbale zolowa.+ Kenako iye anamaliza+ ntchito yonse imene anali kugwirira Mfumu Solomo, yokhudza nyumba ya Yehova. 41 Anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa+ imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo, ndi maukonde awiri+ okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pamwamba pa zipilalazo. 42 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja, mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija. 43 Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pazotengerazo, 44 thanki imodzi,+ ng’ombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+ 45 ndowa, mafosholo, mbale zolowa, ndi ziwiya zina zonse.+ Hiramu anapanga zinthu zimenezi ndi mkuwa wonyezimira. Anapangira Mfumu Solomo kuti aziike m’nyumba ya Yehova. 46 Mfumuyo inaumbira zinthu zimenezi m’chikombole chadongo, m’Chigawo* cha Yorodano,+ pakati pa Sukoti+ ndi Zeretani.+

47 Solomo sanayeze ziwiya zonse+ chifukwa zinali zochuluka kwambiri.+ Mkuwawo sunadziwike kulemera kwake.+ 48 M’kupita kwa nthawi, Solomo anapanga ziwiya zonse za panyumba ya Yehova, za paguwa lansembe+ lagolide, ndi za patebulo+ limene ankaikapo mkate wachionetsero. 49 Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino,+ n’kukaziika pafupi ndi chipinda chamkati, zisanu mbali ya kudzanja lamanja, zisanu mbali ya kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa+ agolide, nyale+ zagolide, zopanira+ zagolide zozimitsira nyale, 50 mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ makapu,+ ndi zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko+ za chipinda chamkati, kutanthauza Chipinda Choyera Koposa, ndiponso molowa miyendo ya zitseko+ za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide.

51 Pa mapeto pake, Mfumu Solomo inamaliza+ ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene inayenera kugwira. Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zonse zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Anatenga siliva, golide, ndi ziwiya zina n’kukaziika mosungira chuma cha panyumba ya Yehova.+

8 Pa nthawi imeneyo Solomo+ anauza akulu,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a makolo+ a ana a Isiraeli, kuti asonkhane+ kwa Mfumu Solomo ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa la pangano+ la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+ 2 Choncho anthu onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa Mfumu Solomo pachikondwerero+ cha m’mwezi wa Etanimu, womwe ndi mwezi wa 7.+ 3 Akulu onse a Isiraeli anabwera, ndipo ansembe anayamba kunyamula+ Likasa.+ 4 Ansembe ndi Alevi+ ananyamula+ likasa la Yehova, chihema+ chokumanako,+ ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali m’chihemacho. 5 Mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Isiraeli, onse amene anabwera atawaitana, anafika pamaso pa Likasa n’kuyamba kupereka nsembe+ zambiri za nkhosa ndi ng’ombe, zomwe sanathe kuziwerenga chifukwa chochuluka.+

6 Kenako ansembe anabweretsa likasa+ la pangano la Yehova kumalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+

7 Akerubiwo anatambasulira mapiko awo pamwamba pa malo okhala Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba pa Likasa ndi mitengo yake yonyamulira.+ 8 Koma mitengo yonyamulirayo+ inali yaitali, moti nsonga zake zinkaoneka kuchokera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinali kuoneka kunja. Mitengo yonyamulirayo ikadali pomwepo mpaka lero.+ 9 Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo+ ku Horebe. Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+

10 Tsopano ansembe atatuluka m’malo oyera, mtambo+ unadzaza nyumba ya Yehova. 11 Chifukwa cha mtambowo, ansembewo+ analephera kupitiriza kutumikira,+ popeza ulemerero+ wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehovayo.+ 12 Pa nthawi imeneyo Solomo anati: “Yehova anati adzakhala mu mdima wandiweyani.+ 13 Ine ndakwanitsa kukumangirani nyumba yomwe ndi malo anu okhalamo okwezeka,+ malo okhazikika+ oti mukhalemo mpaka kalekale.”+

14 Kenako mfumu inatembenuka n’kuyang’ana anthuwo. Ndiyeno inayamba kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli. Pamenepo n’kuti mpingo wonse wa Isiraeli utaimirira. 15 Mfumuyo inapitiriza kuti: “Adalitsike Yehova+ Mulungu wa Isiraeli, amene analankhula ndi pakamwa pake kwa Davide+ bambo anga, ndipo ndi dzanja lake wakwaniritsa zimene ananena,+ zakuti, 16 ‘Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisiraeli m’dziko la Iguputo, sindinasankhe+ mzinda m’mafuko onse a Isiraeli woti iwo amangeko nyumba+ ya dzina langa+ kuti likhale kumeneko. Koma ndidzasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+ 17 Ndipo bambo anga Davide, anafuna mumtima mwawo kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 18 Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Popeza unafuna mumtima mwako kumanga nyumba ya dzina langa, unachita bwino chifukwa unafuna mumtima mwako kuchita zimenezi.+ 19 Koma iweyo sumanga nyumbayi, m’malomwake mwana wako wamwamuna wotuluka m’chiuno mwako ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 20 Yehova anakwaniritsa mawu amene ananena,+ kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga n’kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli,+ monga momwe Yehova ananenera, ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 21 Komanso kuti m’nyumbamo ndisankhemo malo oika Likasa, lomwe muli pangano+ la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.”

22 Tsopano Solomo anaimirira kutsogolo kwa guwa lansembe+ la Yehova pamaso pa mpingo wonse wa Isiraeli. Kenako anatambasula manja ake n’kuwakweza kumwamba.+ 23 Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu+ amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse,+ inu mumawasungira pangano ndi kukoma mtima kosatha.+ 24 Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga. Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 25 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga, pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako asamale mayendedwe awo mwa kuyenda pamaso panga monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’ 26 Tsopano inu Mulungu wa Isiraeli, lonjezo lanu+ limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga, likwaniritsidwe chonde.

27 “Koma kodi Mulungu angakhaledi padziko lapansi?+ Taonani! Kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba,+ simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba+ imene ndamangayi? 28 Mutembenukire ku pemphero+ la mtumiki wanu ndi pempho lake lopempha chifundo,+ inu Yehova Mulungu wanga. Mverani kulira kwanga kochonderera ndi pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero.+ 29 Maso anu akhale akuyang’ana+ nyumba ino usiku ndi usana. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala kumeneko,’+ kuti mumvere pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana kumalo ano.+ 30 Mumve pemphero lopempha chifundo+ la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisiraeli, limene angapemphere atayang’ana malo ano. Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+

31 “Munthu akachimwira mnzake,+ wochimwiridwayo n’kulumbiritsa*+ wochimwayo pofuna kutsimikiza kuti sanachimwedi, ndiyeno wochimwayo akabwera patsogolo pa guwa lansembe m’nyumba ino chifukwa cha zimene analumbira, 32 inu mumve muli kumwamba ndipo muchitepo kanthu mwa kusonyeza amene ali wolakwa pom’bwezera mogwirizana ndi njira yake,+ ndi kusonyeza amene ali wolungama+ pom’patsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo chake.+

33 “Anthu anu Aisiraeli akagonja kwa adani+ awo chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno akabwerera kwa inu+ n’kutamanda dzina lanu+ ndi kupemphera+ ndiponso kupempha kwa inu kuti muwachitire chifundo m’nyumba ino,+ 34 inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la anthu anu Aisiraeli,+ ndi kuwabwezeretsa+ kudziko limene munapatsa makolo awo.+

35 “Kumwamba kukatsekeka, mvula n’kumakanika kugwa+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno iwo n’kupemphera atayang’ana malo ano,+ ndi kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya tchimo lawo chifukwa choti mwakhala mukuwasautsa,+ 36 inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisiraeli, popeza mumawaphunzitsa+ njira yabwino yoti ayendemo.+ Mubweretse mvula+ padziko lanu, limene mwapatsa anthu anu monga cholowa.

37 “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo, ndiponso kukagwa mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse, 38 ndiyeno anthuwo akapereka pemphero lililonse,+ pempho lililonse lopempha chifundo+ limene munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli angapemphe,+ chifukwa aliyense wa iwo akudziwa ululu wa mumtima mwake,+ ndipo iwo akatambasula manja awo kuwalozetsa kunyumba ino,+ 39 inuyo mumve muli kumwamba,+ malo anu okhala okhazikika+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu.+ Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inuyo nokha mumadziwa bwino mtima wa ana onse a anthu).+ 40 Muchite zimenezi n’cholinga choti iwo akuopeni,+ masiku onse amene angakhale ndi moyo padziko limene munapatsa makolo athu.+

41 “Komanso mlendo+ amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu+ 42 (popeza adzamva za dzina lanu lalikulu,+ za dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka), ndipo wabwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+ 43 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+

44 “Anthu anu akapita kunkhondo+ kukamenyana ndi adani awo kumene inuyo mwawatumiza,+ ndipo akapemphera+ kwa Yehova atayang’ana kumzinda umene mwasankha+ ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 45 inuyo mumve muli kumwamba pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+

46 “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa adani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko la adani, lakutali kapena lapafupi,+ 47 ndiyeno iwo n’kuzindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo+ n’kulapa,+ ndipo akapempha+ chifundo kwa inu m’dziko la adani awo amene awagwira,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 48 n’kubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, m’dziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayang’ana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, kumzinda umene mwasankha ndi nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 49 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.+ Mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+ 50 Mukhululukire+ anthu anu amene anakuchimwirani.+ Muwakhululukirenso chifukwa cha malamulo anu onse amene anaphwanya,+ komanso owagwirawo akamawaona azikhudzidwa mtima+ ndi kuwachitira chisoni, 51 (popeza iwo ndi anthu anu ndi cholowa chanu,+ amene munawatulutsa ku Iguputo,+ kuwachotsa m’ng’anjo yachitsulo).+ 52 Maso anu aone pempho lopempha chifundo la mtumiki wanu, ndi pempho lopempha chifundo+ la anthu anu Aisiraeli, mwa kuwamvera zopempha zawo zonse zimene angakupempheni.+ 53 Pakuti inuyo munawapatula pakati pa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi+ kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munalankhulira kudzera mwa Mose+ mtumiki wanu, pamene munali kutulutsa makolo athu ku Iguputo, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.”

54 Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera kwa Yehova pemphero lonseli, ndi pempho lopempha chifundo, anaimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova popeza nthawi yonseyi anali chogwada,+ manja ake atawatambasulira kumwamba.+ 55 Anaimirira+ n’kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli ndi mawu okweza, akuti: 56 “Adalitsike Yehova+ amene wapatsa anthu ake Aisiraeli malo ampumulo, monga mwa zonse zimene analonjeza.+ Palibe mawu ndi amodzi omwe+ amene sanakwaniritsidwe pa malonjezo ake onse abwino amene analonjeza kudzera mwa Mose mtumiki wake.+ 57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe+ monga mmene anakhalira ndi makolo athu.+ Asatisiye kapena kutitaya.+ 58 Alozetse mtima wathu+ kwa iye kuti tiyende m’njira zake zonse+ ndi kusunga malamulo ake,+ malangizo ake,+ ndi zigamulo zake,+ zimene analamula makolo athu. 59 Mawu angawa amene ndanena popempha chifundo pamaso pa Yehova, azikumbukiridwa+ ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti aonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli, monga momwe kungafunikire tsiku+ ndi tsiku. 60 Atero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe+ kuti Yehova ndi Mulungu woona.+ Palibenso wina.+ 61 Mutumikire Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathunthu+ mwa kuyenda motsatira malangizo ake ndi kusunga malamulo ake, monga mmene mukuchitira lero.”

62 Mfumuyo ndi Aisiraeli onse amene anali nayo anayamba kupereka nsembe yaikulu pamaso pa Yehova.+ 63 Solomo anapereka nsembe zachiyanjano+ zimene anayenera kupereka kwa Yehova. Anapereka ng’ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000+ kuti mfumuyo ndi ana onse a Isiraeli atsegulire+ nyumba ya Yehova. 64 Tsiku limenelo, pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova+ panayenera kupatulidwa ndi mfumu, chifukwa inafunika kuperekerapo nsembe yopsereza, nsembe yambewu, ndi mafuta a nsembe zachiyanjano. Inatero popeza guwa lansembe lamkuwa+ limene lili pamaso pa Yehova linachepa, ndipo nsembe yopsereza, nsembe yambewu, ndi mafuta+ a nsembe zachiyanjano sizikanakwanapo. 65 Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero+ pamodzi ndi Aisiraeli onse. Unali mpingo waukulu+ wa anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira polowera ku Hamati+ n’kutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ Anachita chikondwererochi pamaso pa Yehova Mulungu wathu masiku 7, ndi masiku enanso 7.+ Onse pamodzi masiku 14. 66 Pa tsiku la 8 Solomo anauza anthuwo kuti azipita,+ ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo n’kuyamba kupita kwawo. Anapita akusangalala,+ chimwemwe chitadzaza mumtima,+ chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli.

9 Solomo atangomaliza kumanga nyumba+ ya Yehova ndi nyumba ya mfumu+ ndiponso chinthu chilichonse chimene anafuna kupanga,+ 2 Yehova anaonekera kwa iye kachiwiri, mofanana ndi momwe anamuonekera ku Gibeoni.+ 3 Ndipo Yehova anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndi pempho lako lopempha chifundo kwa ine. Ndayeretsa+ nyumba imene wamangayi mwa kuikapo dzina langa+ mpaka kalekale, ndipo maso anga+ ndi mtima wanga adzakhala pamenepo nthawi zonse.+ 4 Iweyo ukayenda+ pamaso panga monga momwe Davide+ bambo ako anayendera, yemwe anali ndi mtima wosagawanika+ ndipo anayenda mowongoka,+ ukachita mogwirizana ndi zonse zimene ndinakulamula,+ komanso ukasunga malangizo anga+ ndi zigamulo zanga,+ 5 inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu ufumu wa Isiraeli mpaka kalekale, monga momwe ndinalonjezera Davide bambo ako kuti, ‘Munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ 6 Koma inuyo ndi ana anu mukadzabwerera n’kusiya kunditsatira,+ osasunga malamulo anga amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina+ ndi kuigwadira, 7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu. 8 Nyumba iyi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa+ ndi kuimba mluzu n’kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+ 9 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake, anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira. N’chifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+

10 Ndiyeno pamapeto pa zaka 20 zimene Solomo anamanga nyumba ziwirizo, nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu,+ 11 Mfumu Solomo anapatsa Hiramu mizinda 20 m’dera la Galileya.+ (Hiramu+ mfumu ya Turo anathandiza Solomo+ ndi matabwa a mkungudza, matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, ndi golide yense amene anafuna.)+ 12 Choncho Hiramu anachoka ku Turo kupita kukaona mizinda imene Solomo anamupatsa, koma sinamusangalatse ataiona.+ 13 Ndipo anati: “Kodi mizinda wandipatsayi ndi yamtundu wanji m’bale wanga?” Chotero mizindayo inatchedwa Dziko la Kabulu* mpaka lero.

14 Pa nthawi imeneyo, Hiramu anatumiza kwa mfumuyo golide wokwana matalente* 120.+

15 Mfumu Solomo inaitana anthu ogwira ntchito yokakamiza+ kuti adzamange nyumba ya Yehova,+ nyumba yake, Chimulu cha Dothi,*+ khoma+ lozungulira Yerusalemu, ndiponso mizinda ya Hazori,+ Megido,+ ndi Gezeri.+ 16 (M’mbuyomo, Farao mfumu ya Iguputo inabwera n’kulanda mzinda wa Gezeri n’kuutentha ndi moto. Akanani+ okhala mumzindawo inawapha. Kenako inaupereka kwa mwana wake wamkazi+ monga mphatso pamene anali kukwatiwa ndi Solomo.) 17 Solomo anamanganso Gezeri, Beti-horoni Wakumunsi,+ 18 Baalati,+ ndi Tamara m’chipululu cha m’dzikolo. 19 Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu,+ mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi, ndiponso zilizonse zimene iye anakonda+ kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni, ndi m’dziko lonse limene ankalamulira. 20 Anthu onse otsala a Aamori,+ Ahiti,+ Aperezi,+ Ahivi,+ ndi Ayebusi,+ amene sanali ana a Isiraeli,+ 21 ana awo amene anatsala m’dzikomo, amene ana a Isiraeli analephera kuwawononga,+ Solomo anali kuwagwiritsa ntchito yaukapolo. Anthuwa akupitiriza kugwira ntchito yotere kufikira lero.+ 22 Palibe ana a Isiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo,+ chifukwa iwo anali ankhondo ake, atumiki ake, akalonga ake, asilikali othandiza pa magaleta, ndiponso atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta, ndi a amuna ake okwera pamahatchi.+ 23 Panali akuluakulu oyang’anira nduna okwana 550 amene ankayang’anira ntchito ya Solomo. Iwowa anali akapitawo oyang’anira anthu ogwira ntchito.+

24 Mwana wamkazi wa Farao+ anachoka ku Mzinda wa Davide+ n’kukakhala kunyumba yake imene Solomo anam’mangira. Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+

25 Katatu+ pachaka, Solomo ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano paguwa lansembe limene anamangira Yehova.+ Ankapereka nsembe zautsi paguwa lansembe+ lomwe linali pamaso pa Yehova, ndipo anamaliza kumanga nyumbayo.+

26 Panali zombo zimene Mfumu Solomo inapanga ku Ezioni-geberi,+ pafupi ndi Eloti,+ pagombe la Nyanja Yofiira m’dziko la Edomu.+ 27 M’zombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake+ omwe anali amalinyero odziwa za panyanja, pamodzi ndi antchito a Solomo. 28 Iwo ankapita ku Ofiri+ n’kukatenga golide wokwana matalente 420,+ n’kubwera naye kwa Mfumu Solomo.

10 Mfumukazi ya ku Sheba+ inali kumva za Solomo, ndi zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+ 2 Mfumukaziyo inafika ku Yerusalemu ndi anthu ambiri oiperekeza.+ Inabwera ndi ngamila+ zitanyamula mafuta a basamu,+ golide wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali. Inafika kwa Solomo n’kuyamba kunena zonse zimene zinali kumtima kwake.+ 3 Solomo anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse.+ Panalibe chimene mfumuyo inalephera kuyankha.+

4 Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru zonse za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+ 5 chakudya cha patebulo pake,+ mmene atumiki ake anali kukhalira pa nthawi ya chakudya, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuchitira zinthu, zovala zawo, zakumwa zake,+ ndi nsembe zake zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse, inazizira nkhongono ndipo inasowa chonena.+ 6 Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani za zochita zanu ndi nzeru zanu zimene ndinamva kudziko langa, n’zoonadi.+ 7 Sindinakhulupirire mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga, ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe.+ Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa zinthu zimene ndinamva.+ 8 Odala anthu anu,+ odala+ atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.+ 9 Adalitsike+ Yehova Mulungu wanu, amene wasangalala+ nanu mwa kukuikani pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Popeza Yehova adzakonda Isiraeli mpaka kalekale,+ wakuikani kuti mukhale mfumu+ kuti muzipereka zigamulo+ ndi kuchita chilungamo.”+

10 Kenako mfumukaziyo inapatsa+ mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali. Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.

11 Zombo+ za Hiramu zimene zinabweretsa golide kuchokera ku Ofiri,+ zinabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ochuluka zedi ndi miyala yamtengo wapatali.+ 12 Mfumuyo inapanga zochirikizira nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu, pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo. Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba. Matabwa a m’bawa ochuluka chonchi sanayambe abwerapo kapena kuonedwapo mpaka lero.

13 Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha, kuwonjezera pa zimene Mfumu Solomo inam’patsa malinga ndi kuwolowa manja+ kwa mfumuyo. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+

14 Golide+ amene ankabwera kwa Solomo chaka chimodzi, anali wolemera matalente 666,*+ 15 osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda, ndi phindu lochokera kwa amalonda, komanso golide wochokera kwa mafumu onse+ a Aluya,+ ndi kwa abwanamkubwa a m’dzikolo.

16 Mfumu Solomo inapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chachikulu chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 17 Inapanganso zishango 300 zing’onozing’ono za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chaching’ono chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.)+ Kenako mfumuyo inaika zishangozi m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+

18 Itatero, mfumuyo inapanga mpando wachifumu+ waukulu waminyanga ya njovu,+ n’kuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 19 Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Kuseri kwa mpando wachifumuwo kunali chotchingira chozungulira. Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira.+ 20 Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango itaimirira, mbali iyi ndi iyi. Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.+

21 Ziwiya zonse zomweramo Mfumu Solomo zinali zagolide, ndipo ziwiya zonse za m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali za golide woyenga bwino.+ Panalibe chiwiya chasiliva. Siliva sankaoneka ngati kanthu m’masiku a Solomo. 22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide,+ siliva, minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.

23 Chotero Mfumu Solomo inali yolemera kwambiri+ ndiponso yanzeru+ kwambiri kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 24 Anthu onse a padziko lapansi ankafuna kuonana ndi Solomo, kuti amve nzeru zake zimene Mulungu anaika mumtima mwake.+ 25 Aliyense anali kubweretsa mphatso+ chaka chilichonse+ monga zinthu zasiliva,+ zinthu zagolide, zovala, zida zankhondo,+ mafuta a basamu, mahatchi, ndi nyulu.+

26 Solomo anali kusonkhanitsa magaleta ambiri ndi mahatchi ankhondo, ndipo anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi ankhondo 12,000.+ Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yake yosungiramo magaleta ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu.+

27 Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva akhale wochuluka kwambiri ngati miyala,+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu ya ku Sefela.+

28 Panalinso mahatchi amene Solomo anali kugula kuchokera ku Iguputo, ndipo gulu la amalonda a mfumu ndilo linali kugula mahatchiwo m’magulumagulu.+ 29 Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti+ ndi mafumu a ku Siriya anali kuchitira. Mafumuwa ankagwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.

11 Mfumu Solomo inakonda akazi ambiri achilendo+ kuphatikiza pa mwana wamkazi wa Farao.+ Inakonda akazi achimowabu,+ achiamoni,+ achiedomu,+ achisidoni,+ ndi achihiti.+ 2 Akaziwa anali ochokera m’mitundu imene Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Musamapite pakati pawo+ ndipo iwonso asamabwere pakati panu, chifukwa ndithu adzapotoza mitima yanu kuti itsatire milungu yawo.”+ Amenewa ndi amene Solomo anaumirira+ kuwakonda. 3 Choncho iye anali ndi akazi olemekezeka 700, ndi akazi ena apambali 300. M’kupita kwa nthawi,+ akazi amenewa anapotoza mtima wa Solomo. 4 Pamene iye anali kukalamba,+ akazi ake anali atapotoza+ mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina.+ Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu+ monga mmene anachitira Davide bambo ake. 5 Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni, ndi Milikomu,+ chonyansa cha Aamoni. 6 Chotero Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa+ m’maso mwa Yehova, ndipo sanatsatire Yehova ndi mtima wonse ngati Davide bambo ake.+

7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni. 8 Izi n’zimene anachitira akazi ake onse achilendo+ amene anali kupereka nsembe zautsi ndi nsembe zina kwa milungu yawo.+

9 Koma Yehova anamukwiyira kwambiri+ Solomo chifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene anamuonekera kawiri konse.+ 10 Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatire milungu ina,+ koma iye sanasunge zimene Yehova analamula. 11 Tsopano Yehova anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiponso sunasunge pangano langa ndi malamulo amene ndinakulamula, ndidzang’amba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe, ndipo ndithu ndidzaupereka kwa mtumiki wako.+ 12 Komabe, sindichita zimenezi iwe uli ndi moyo+ chifukwa cha bambo ako Davide.+ Ufumuwu ndidzaung’amba ndi kuuchotsa m’manja mwa mwana wako,+ 13 koma sindidzauchotsa wonse.+ Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga+ ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha.”+

14 Kenako Yehova anasankha munthu woti azilimbana+ ndi Solomo.+ Munthuyo dzina lake linali Hadadi, Mwedomu, mbadwa ya mfumu, ndipo anali kukhala ku Edomu.+ 15 Pa nthawi imene Davide anawononga Edomu,+ Yowabu, mkulu wa asilikali, anapita kukafotsera anthu amene anaphedwa. Kumeneko anayambanso kupha mwamuna aliyense wa ku Edomu.+ 16 (Yowabu ndi Aisiraeli onse anakhala kumeneko miyezi 6, kufikira atapha mwamuna aliyense mu Edomu.) 17 Koma Hadadi pamodzi ndi amuna ena achiedomu omwe anali atumiki a bambo ake, anathawira ku Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Hadadi ali kamnyamata. 18 Iwo ananyamuka ku Midiyani+ n’kukafika ku Parana.+ Kumeneko anatenga anthu ena n’kukafika ku Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anam’patsa nyumba Hadadi, ndiponso chakudya ndi malo. 19 Farao anapitiriza kum’komera mtima Hadadi,+ moti mpaka anam’patsa mkazi.+ Mkaziyo anali mng’ono wake wa Takipenesi, mkazi wa Farao. 20 M’kupita kwa nthawi, mng’ono wake wa Takipenesi anaberekera Hadadi mwana wamwamuna dzina lake Genubati. Takipenesi anamusiyitsa kuyamwa+ mwanayo n’kuyamba kumusamalira m’nyumba ya Farao. Genubati anapitiriza kukhala m’nyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao.

21 Hadadi ali ku Iguputo, anamva kuti Davide anamwalira ndipo anagona m’manda pamodzi ndi makolo ake,+ ndiponso kuti Yowabu mkulu wa asilikali anamwalira.+ Choncho Hadadi anauza Farao kuti: “Ndiloleni ndizipita+ kwathu.” 22 Koma Farao anamufunsa kuti: “Kodi ukusowa chiyani pamene ukukhala ndi ine kuti ufune kupita kwanu?” Hadadi anayankha kuti: “Palibe chimene ndikusowa, koma chonde ndiloleni ndizipita.”

23 Mulungu anasankha munthu winanso woti azilimbana+ ndi Solomo. Munthuyo anali Rezoni mwana wa Eliyada, yemwe anathawa kwa mbuye wake Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba.+ 24 Davide atapha+ anthu a ku Zoba, Rezoni anayamba kusonkhanitsa anthu kumbali yake, ndipo anakhala mtsogoleri wa gulu la achifwamba. Chotero iye ndi gulu lakelo anapita kukakhala ku Damasiko,+ n’kuyamba kulamulira kumeneko. 25 Rezoni analimbana ndi Isiraeli masiku onse a Solomo,+ ndipo anali kuchitira Aisiraeli zoipa monga momwe ankachitira Hadadi. Rezoni ankaipidwa kwambiri+ ndi Isiraeli pa nthawi imene iye anali kulamulira ku Siriya.

26 Panalinso Yerobowamu,+ mwana wa Nebati, wa fuko la Efuraimu, wa ku Zereda. Iye anali mtumiki wa Solomo.+ Mayi ake anali mkazi wamasiye dzina lake Zeruwa. Nayenso Yerobowamu anayamba kuukira mfumu.+ 27 Iye anaukira mfumu pa chifukwa ichi: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa Davide bambo ake.+ 28 Yerobowamu anali mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima.+ Solomo ataona kuti mnyamatayo anali wogwira ntchito molimbika,+ anamuika kukhala woyang’anira+ ntchito yonse yokakamiza+ ya kunyumba ya Yosefe.+ 29 Pa nthawi imeneyo, Yerobowamu anatuluka mu Yerusalemu, ndipo Ahiya+ Msilo+ yemwe anali mneneri, anam’peza panjira. Ahiya anali atavala chovala chatsopano. Awiriwo anali okhaokha kumeneko. 30 Ndiyeno Ahiya anatenga chovala chatsopano chimene anavala chija n’kuching’ambang’amba+ zidutswa zokwana 12.+ 31 Atatero, anamuuza Yerobowamu kuti:

“Tengapo zidutswa 10, pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wati, ‘Ndikung’amba ufumuwu kuuchotsa m’manja mwa Solomo, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko 10.+ 32 Fuko limodzi+ lipitiriza kukhala lake chifukwa cha mtumiki wanga Davide,+ ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu+ umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli. 33 Ndichita zimenezi chifukwa iwo andisiya ine+ n’kuyamba kugwadira Asitoreti+ mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi+ mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu+ mulungu wa ana a Amoni. Sanayende m’njira zanga mwa kuchita choyenera pamaso panga ndi kutsatira malamulo anga ndi zigamulo zanga monga anachitira Davide bambo a Solomo. 34 Koma sindidzachotsa ufumu wonse m’manja mwake. Ndidzamuika kukhala mtsogoleri masiku onse a moyo wake chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndinamusankha,+ pakuti Davide anasunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. 35 Ndidzachotsadi ufumuwu m’manja mwa mwana wake ndi kuupereka kwa iwe, ndithu ndidzakupatsa mafuko 10.+ 36 Mwana wake ndidzam’patsa fuko limodzi kuti Davide mtumiki wanga apitirize kukhala ndi nyale pamaso panga mu Yerusalemu,+ mzinda umene ndausankha kuti ndiikepo dzina langa.+ 37 Ndidzasankha iweyo, ndipo udzalamuliradi zonse zimene moyo wako umakhumba.+ Udzakhaladi mfumu ya Isiraeli. 38 Ukamvera malamulo anga onse, ndipo ukayenda m’njira zanga ndi kuchita zoyenera pamaso panga, mwa kusunga malamulo anga monga anachitira Davide mtumiki wanga,+ inenso ndidzakhala nawe.+ Ana ako adzalamulira kwa nthawi yaitali mofanana ndi ana a Davide,+ ndipo ndidzakupatsa Isiraeli. 39 Ndidzachititsa manyazi ana a Davide chifukwa cha zoipa zimene anachita,+ koma osati nthawi zonse.’”+

40 Chotero Solomo anayamba kufunafuna kupha Yerobowamu.+ Choncho Yerobowamu ananyamuka n’kuthawira+ ku Iguputo kwa Sisaki,+ mfumu ya Iguputo. Anakhala ku Iguputoko mpaka Solomo atamwalira.

41 Nkhani zina zokhudza Solomo ndi zonse zimene anachita, ndiponso nzeru zake, zinalembedwa m’buku lonena za Solomo. 42 Masiku onse amene Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu anakwana zaka 40.+ 43 Kenako Solomo anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide+ bambo ake. Kenako mwana wake Rehobowamu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.

12 Rehobowamu+ anapita ku Sekemu,+ chifukwa kumeneko n’kumene Aisiraeli onse anasonkhana kuti akamulonge ufumu. 2 Yerobowamu+ mwana wa Nebati anamva zimenezi akadali ku Iguputo, (pajatu anathawa Mfumu Solomo n’kukakhala ku Iguputo),+ 3 ndipo anthu anatumiza uthenga womuitana. Kenako Yerobowamu ndi mpingo wonse wa Isiraeli anabwera n’kuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:+ 4 “Bambo anu anaumitsa goli lathu. Tsopano inuyo mufewetse+ ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera+ limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”+

5 Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye kwa masiku atatu, ndipo mukabwerenso kwa ine.”+ Anthuwo anapitadi. 6 Ndiyeno Mfumu Rehobowamu inafunsira nzeru kwa akulu+ amene anali kutumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Inawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”+ 7 Iwo anaiuza kuti: “Ngati lero mukufuna kuti mukhale mtumiki wa anthuwa ndi kuwatumikira,+ muwayankhe ndi mawu abwino,+ ndipo iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”+

8 Koma iye sanamvere malangizo ochokera kwa akulu aja, m’malomwake anayamba kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi,+ omwe anali kumutumikira.+ 9 Iye anawafunsa kuti: “Kodi mungapereke malangizo+ otani kuti tiwayankhe anthuwa amene andipempha kuti, ‘Fewetsani goli limene bambo anu anatisenzetsa’?”+ 10 Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Izi n’zimene mukanene+ kwa anthu awa amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsireko.’ Muwauze kuti, ‘Chala changa chaching’ono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga.+ 11 Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo.+ Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”+

12 Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, monga momwe mfumuyo inanenera kuti: “Mukabwerenso kwa ine pa tsiku lachitatu.”+ 13 Mfumuyo inayamba kuyankha anthuwo mwaukali+ ndipo sinamvere malangizo ochokera kwa akulu amene anailangiza aja.+ 14 Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja+ anaipatsa. Inati: “Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera, koma ine ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+ 15 Mfumuyo sinamvere anthuwo+ chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Yehova,+ kuti akwaniritse mawu amene Yehovayo analankhula+ kwa Yerobowamu mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya+ Msilo.

16 Aisiraeli onse ataona kuti mfumuyo sinawamvere, anaiyankha kuti: “Tili ndi gawo lanji mwa Davide?+ Ife tilibe cholowa mwa mwana wa Jese. Pitani kwa milungu yanu+ Aisiraeli. Tsopano iwe Davide,+ uzisamalira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, anayamba kubwerera kumahema awo. 17 Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira ana a Isiraeli amene anali kukhala m’mizinda ya ku Yuda.+

18 Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Adoramu+ amene anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yokakamiza,+ koma Aisiraeli onse anam’ponya miyala+ n’kumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inatha kukwera galeta n’kuthawira ku Yerusalemu. 19 Ndipo Aisiraeli anapitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.+

20 Aisiraeli onse atangomva kuti Yerobowamu wabwera, nthawi yomweyo anatumiza uthenga womuitanira kumene anasonkhana, ndipo anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse.+ Palibenso amene ankatsatira nyumba ya Davide kupatula fuko la Yuda lokha.+

21 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi nyumba ya Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu mwana wa Solomo. 22 Kenako mawu a Mulungu woona anafikira Semaya+ munthu wa Mulungu woona,+ kuti: 23 “Kauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda, ndi nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini, ndi anthu ena onse kuti, 24 ‘Yehova wati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”’”+ Choncho anamvera mawu a Yehova+ n’kubwerera kwawo malinga ndi mawu a Yehova.+

25 Yerobowamu anamanga mzinda wa Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, n’kuyamba kukhala kumeneko. Kenako anachoka kumeneko n’kupita kukamanga mzinda wa Penueli.+ 26 Ndiyeno Yerobowamu anayamba kunena mumtima mwake kuti:+ “Tsopano ufumuwu ubwerera kunyumba ya Davide.+ 27 Anthu awa akapitiriza kupita kukapereka nsembe kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu,+ mtima wawo ubwerera kwa mbuye wawo Rehobowamu mfumu ya Yuda, ndipo ineyo adzandipha+ n’kubwerera kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.” 28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+ 29 Ndiyeno chifaniziro cha ng’ombe chimodzi anakachiika ku Beteli,+ china anakachiika ku Dani.+ 30 Chinthu chimenechi chinakhala chochimwitsa anthu.+ Anthuwo anali kukafika mpaka ku Dani kukaima pamaso pa chifaniziro cha mwana wa ng’ombecho.

31 Yerobowamu anayamba kumanga akachisi m’malo okwezeka.+ Ndiyeno anasankha anthu wamba, anthu amene sanali ana a Levi, n’kuwaika kuti akhale ansembe.+ 32 M’mwezi wa 8, pa tsiku la 15 la mweziwo, Yerobowamu anachita chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda.+ Anachita chikondwererochi kuti apereke nsembe kwa ana a ng’ombe amene anawapanga, paguwa lansembe limene analimanga ku Beteli.+ M’malo okwezeka a ku Beteli amene anamanga, anaikako ansembe kuti azitumikira. 33 Yerobowamu anapereka nsembe pa tsiku la 15, m’mwezi wa 8 womwe anausankha yekha.+ Anapereka nsembezo paguwa limene anamanga ku Beteli. Ndipo anakonzera chikondwerero ana a Isiraeli ndi kupereka nsembe zautsi kuti afukize paguwalo.+

13 Tsopano panali munthu+ wa Mulungu amene anatumidwa+ ndi Yehova kuchokera ku Yuda kupita ku Beteli. Kumeneko iye anapeza Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa lansembe+ kuti afukize nsembe yautsi.+ 2 Ndiyeno anafuulira guwa lansembelo mawu ochokera kwa Yehova oitanira tsoka, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Ndithu adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akufukiza nsembe yautsi pa iwe, n’kuwapereka nsembe pa iwe. Iye adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+ 3 Kenako munthu wa Mulunguyo anapereka chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ pa tsikulo. Iye anati: “Nachi chizindikiro cholosera zam’tsogolo chimene Yehova wanena: Guwa lansembeli ling’ambika pakati, ndipo phulusa losakanizika ndi mafuta limene lili paguwali litayika.”

4 Mfumu Yerobowamu itangomva mawu oitanira tsoka amene munthu wa Mulunguyo ananena kwa guwa lansembe la ku Beteli, nthawi yomweyo inatambasula dzanja lake kulichotsa paguwa lansembe, n’kunena kuti: “Amuna inu, m’gwireni uyu!”+ Itangotero dzanja limene inatambasula kuloza munthu wa Mulungu uja linauma, ndipo sinathenso kulibweza.+ 5 Guwa lansembelo linang’ambika pakati moti phulusa losakanizika ndi mafuta linatayika kuchokera paguwalo. Izi zinachitika mogwirizana ndi chizindikiro cholosera zam’tsogolo chimene munthu wa Mulungu woonayo anapereka, malinga ndi mawu a Yehova.+

6 Tsopano mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde! Khazikani pansi mtima wa Yehova Mulungu wanu. Mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woona uja anakhazikadi pansi+ mtima wa Yehova, moti dzanja la mfumu linabwerera mwakale, n’kukhala ngati mmene linalili poyamba.+ 7 Kenako mfumuyo inauza munthuyo kuti: “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya,+ ndiponso ndikakupatseni mphatso.”+ 8 Koma munthu wa Mulungu woona uja anayankha mfumuyo kuti: “Ngakhale mutandipatsa hafu ya nyumba yanu,+ sindingapite nanu+ kukadya chakudya kapena kumwa madzi kwanu kuno. 9 Chifukwa mawu a Yehova andilamula kuti: ‘Usakadye chakudya+ kapena kumwa madzi, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 10 Iye anadutsadi njira ina. Sanadutse njira imene anadzera popita ku Beteliko.

11 Ndiyeno panali mneneri wina wokalamba+ yemwe anali kukhala ku Beteli. Ana ake anabwera n’kuyamba kumufotokozera zonse zimene munthu wa Mulungu woona uja anachita pa tsikulo ku Beteli. Anamuuzanso mawu amene munthuyo anauza mfumu. 12 Pamenepo bamboyu anafunsa anawo kuti: “Munthuyo wadzera njira iti?” Anawo analozera bamboyu njira imene munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja anadzera. 13 Kenako bamboyu anauza anawo kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Anawo anawamangiradi chishalocho,+ ndipo iwo anakwera buluyo.

14 Atatero, analondola munthu wa Mulungu woona uja, ndipo anam’peza atakhala pansi pa mtengo waukulu.+ Ndiyeno anafunsa munthuyo kuti: “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu woona amene wachokera ku Yuda?”+ Munthuyo anayankha kuti: “Ndine amene.” 15 Kenako anamuuza munthuyo kuti: “Tiye kunyumba ukadye chakudya.” 16 Koma munthuyo anati: “Sindingabwerere nanu kapena kupita kunyumba kwanu, ndipo sindingadye nanu chakudya kapena kumwa madzi kwanu kuno.+ 17 Chifukwa mawu ochokera kwa Yehova+ andiuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udzere popita.’”+ 18 Mneneri wokalambayo atamva zimenezi, anati: “Inenso ndine mneneri ngati iweyo. Mngelo+ wandiuza mawu ochokera kwa Yehova akuti, ‘Kam’bweze upite naye kunyumba kwako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” (Anamunamiza.)+ 19 Choncho anabwerera naye kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi kunyumba kwake.+

20 Akudya patebulo, mawu+ a Yehova anafikira mneneri yemwe anabweza munthu wa ku Yuda uja. 21 Ndiyeno anayamba kuuza munthu wa Mulungu woona yemwe anachokera ku Yuda uja, kuti: “Nazi zimene Yehova wanena, ‘Chifukwa chakuti wapandukira+ lamulo la Yehova, ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakulamula,+ 22 koma wabwerera kuti udye chakudya ndi kumwa madzi kumalo amene iye anakuuza kuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi,” mtembo wako sudzaikidwa m’manda a makolo ako.’”+

23 Mneneri wa ku Yuda uja atatha kudya ndi kumwa, nthawi yomweyo mneneri wokalamba uja anamanga chishalo pabulu wa mneneri wa ku Yuda, yemwe anam’bweza uja. 24 Kenako mneneri wa ku Yudayo ananyamuka n’kumapita. Pambuyo pake mkango+ unam’peza panjira n’kumupha,+ ndipo mtembo wake unali pamsewu. Kumbali ina ya mtembowo kunaima bulu uja, ndipo mbali inayi kunaima mkangowo. 25 Tsopano anthu ena amene anali kudutsa, anaona mtembowo uli pamsewupo, mkango utaima pambali pake. Anthuwo atafika mumzinda womwe munali kukhala mneneri wokalamba uja, anafotokoza zomwe anaonazo.

26 Mneneri amene anakabweza munthu uja atamva nkhaniyo, nthawi yomweyo anati: “Ndi munthu wa Mulungu woona uja amene anapandukira lamulo la Yehova.+ Choncho Yehova wam’pereka kwa mkango kuti umugwire n’kumupha, malinga ndi mawu amene Yehova anamuuza.”+ 27 Ndiyeno anauza ana ake kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Choncho ana akewo anam’mangiradi chishalocho.+ 28 Mneneri wokalambayo ananyamuka n’kukapeza mtembo wa munthu uja uli pamsewu, bulu ndi mkango zitaima pambali pake. Mkangowo sunadye mtembowo kapena kupha buluyo.+ 29 Ndiyeno mneneriyo ananyamula mtembo wa munthu wa Mulungu woona uja. Anaukweza pabulu n’kubwerera nawo mpaka kukafika mumzinda wa mneneri wokalambayo, kuti akamulire ndi kumuika m’manda munthuyo. 30 Atatero, mneneri wokalambayo anakaika mtembowo m’manda ake. Ndipo anapitiriza kumulira+ kuti: “Kalanga ine, m’bale wanga!” 31 Atamuika m’manda, mneneri wokalambayo anauza ana ake kuti: “Ine ndikadzamwalira mudzandiike m’manda amene taika munthu wa Mulungu woona uja. Mudzaike mafupa anga pambali pa mafupa ake,+ 32 chifukwa mawu a Yehova oitanira tsoka amene munthu wa Mulungu uja ananena kwa guwa lansembe+ limene lili ku Beteli, ndi kwa akachisi onse a m’malo okwezeka+ amene ali m’mizinda ya ku Samariya,+ ndithu adzakwaniritsidwa.”+

33 Pambuyo pa zimenezi, Yerobowamu sanasiyebe njira yake yoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kukhala ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye anali kum’patsa mphamvu+ mwa kunena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.” 34 Zimenezi zinachimwitsa nyumba yonse ya Yerobowamu,+ ndipo inayenera kuwonongedwa ndi kufafanizidwa padziko lapansi.+

14 Pa nthawi imeneyo, Abiya mwana wamwamuna wa Yerobowamu anadwala.+ 2 Choncho Yerobowamu anauza mkazi wake kuti: “Nyamuka, udzisinthe+ kuti anthu asadziwe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu ndipo upite ku Silo. Kumeneko n’kumene kuli mneneri Ahiya.+ Ameneyo ndiye anandiuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthuwa.+ 3 Utenge mitanda 10 ya mkate,+ makeke, ndi botolo+ la uchi, ndipo ukafike kwa iyeyo.+ Iye ndiye akakuuze zimene zichitikire mnyamatayu.”+

4 Mkazi wa Yerobowamu anachitadi zimenezo. Choncho ananyamuka kupita ku Silo+ n’kukafika kunyumba kwa Ahiya. Ahiyayo sankatha kuona chifukwa maso ake anachita khungu ndi ukalamba.+

5 Yehova anali atauza Ahiya kuti: “Kukubwera mkazi wa Yerobowamu kudzakufunsa za mwana wake, chifukwa mwanayo akudwala. Umuuze zakutizakuti. Zomwe zichitike n’zakuti, akangofika adzisintha kuti asadziwike.”+

6 Choncho Ahiya atangomva phokoso la mapazi a mkazi wa Yerobowamu pamene anali kulowa pakhomo, anayamba kulankhula kuti: “Lowa mkazi wa Yerobowamu.+ N’chifukwa chiyani ukudzisintha kuti usadziwike pamene ine ndatumidwa kwa iwe ndi uthenga wopweteka? 7 Pita, kauze Yerobowamu kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndinakukweza pakati pa anthu ako, kuti ndikuike kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli,+ 8 ndipo ndinang’amba+ ufumuwo kuuchotsa kunyumba ya Davide ndi kuupereka kwa iwe, koma iwe sunakhale ngati Davide mtumiki wanga. Iyeyo anasunga malamulo anga ndi kunditsatira ndi mtima wake wonse mwa kuchita zinthu zoyenera zokhazokha m’maso mwanga.+ 9 Koma iweyo unayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iwe usanakhale. Unadzipangiranso mulungu wina+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula+ kuti undikwiyitse,+ ndipo wandikankhira ineyo kumbuyo kwako.+ 10 Pa chifukwa chimenechi, ndibweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu. Ndithu ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’nyumba ya Yerobowamu, ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake mu Isiraeli.+ Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu,+ monga momwe munthu amasesera ndowe mpaka atakazitaya.+ 11 Munthu wa m’banja la Yerobowamu wofera mumzinda, agalu adzamudya,+ ndipo wofera kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya,+ chifukwa choti Yehova wanena.”’

12 “Iweyo nyamuka pita kunyumba kwako. Mapazi ako akakangolowa mumzinda, mwanayo akamwalira ndithu. 13 Ndipo Aisiraeli onse akamulira+ ndi kumuika m’manda. Iwo akamulira popeza m’banja lonse la Yerobowamu, uyu yekha ndiye adzaikidwe m’manda chifukwa chakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli, wapeza chinachake chabwino mwa yekhayu m’nyumba yonse ya Yerobowamu.+ 14 Yehova adzaika yekha mfumu+ ina yolamulira Isiraeli, yomwe idzafafanize nyumba ya Yerobowamu tsiku limenelo, ndipo ngati atafuna akhoza kuchita zimenezi pompano.+ 15 Yehova adzawonongadi Isiraeli, ndipo zidzakhala ngati mmene bango limagwedezekera m’madzi,+ ndiponso adzazuladi+ Aisiraeli, kuwachotsa padziko labwinoli+ limene anapatsa makolo awo. Ndiyeno adzawabalalitsira+ kutsidya lina la Mtsinje,*+ popeza iwo anapanga mizati yawo yopatulika,+ n’kukwiyitsa+ nayo Yehova. 16 Iye adzasiya Isiraeli+ chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli.”+

17 Atamva zimenezi, mkazi wa Yerobowamu ananyamuka n’kumapita ndipo anafika ku Tiriza.+ Atangofika pakhomo la nyumba yawo, mnyamatayo anamwalira. 18 Choncho anamuika m’manda ndipo Aisiraeli onse anamulira, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.

19 Nkhani zina zokhudza Yerobowamu, momwe anamenyera nkhondo+ ndi momwe analamulirira, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 20 Yerobowamu analamulira zaka 22, kenako anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Nadabu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

21 Rehobowamu+ mwana wa Solomo anali atakhala mfumu ku Yuda. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene anayamba kulamulira, ndipo kwa zaka 17 analamulira ku Yerusalemu, mzinda+ umene Yehova anasankha pakati pa mafuko onse+ a Isiraeli kuti aike dzina lake kumeneko.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama Muamoni.+ 22 Ayuda anapitiriza kuchita zoipa m’maso mwa Yehova,+ moti anamuchititsa+ nsanje kuposa mmene makolo awo anamuchititsira nsanje ndi machimo awo onse amene makolowo anachita.+ 23 Ndipo nawonso anapitiriza kudzimangira malo okwezeka,+ zipilala zopatulika,+ ndi mizati yopatulika+ pamwamba pa phiri lililonse lalitali,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 24 Ngakhalenso mahule aamuna a pakachisi ankapezeka m’dzikomo.+ Anthuwo anachita zinthu zonse zonyansa zimene inkachita mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+

25 Ndiyeno m’chaka chachisanu cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki+ mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu. 26 Iye anatenga chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse+ kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+ 27 Choncho Mfumu Rehobowamu inapanga zishango zamkuwa m’malomwake, ndipo inazipereka kwa akulu a asilikali othamanga,+ omwe anali alonda a pakhomo la nyumba ya mfumu, kuti aziziyang’anira.+ 28 Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikali othamangawo ankanyamula zishangozo, ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.+

29 Nkhani zina zokhudza Rehobowamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’nthawi ya mafumu a Yuda. 30 Ndipo nkhondo inkachitika nthawi zonse pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.+ 31 Pomalizira pake, Rehobowamu anagona ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Mayi ake dzina lawo linali Naama Muamoni.+ Kenako Abiyamu+ mwana wa Rehobowamu anayamba kulamulira m’malo mwake.

15 M’chaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu+ mwana wa Nebati,+ Abiyamu anakhala mfumu ya Yuda.+ 2 Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu.*+ 3 Abiyamu anapitiriza kuyenda m’machimo onse amene bambo ake anachita. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+ 4 Chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anam’patsa nyale+ mu Yerusalemu mwa kukweza mwana wake pambuyo pake, ndiponso kuchititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.+ 5 Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo sanapatuke pa chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake,+ kupatulapo pa nkhani ya Uriya Mhiti.+ 6 Pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu pankachitika nkhondo masiku onse a moyo wa Rehobowamu.+

7 Nkhani zina zokhudza Abiyamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. Pakati pa Abiyamu ndi Yerobowamu, panachitikanso nkhondo.+ 8 Pomalizira pake, Abiyamu anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Asa+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

9 M’chaka cha 20 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda. 10 Analamulira ku Yerusalemu zaka 41. Agogo ake aakazi dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu.+ 11 Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.+ 12 Choncho iye anachotsa mahule aamuna a pakachisi m’dzikolo,+ ndiponso mafano onse onyansa*+ amene makolo ake anapanga.+ 13 Anachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika. Pambuyo pake Asa anagwetsa fanolo n’kukalitentha+ m’chigwa* cha Kidironi.+ 14 Koma iye sanachotse+ malo okwezeka.+ Komabe, Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu masiku ake onse.+ 15 Iye anayamba kubweretsa kunyumba ya Yehova zinthu zimene bambo ake anaziyeretsa, komanso zinthu zimene iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide, ndi ziwiya zina.+

16 Pakati pa Asa ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli, panali kuchitika nkhondo masiku awo onse. 17 Choncho Basa mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda. Kenako anayamba kumanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama,+ kuti anthu asamapite kwa Asa mfumu ya Yuda kapena kubwera kuchokera kwa Asa.+ 18 Asa ataona zimenezi anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi pa chuma cha m’nyumba ya mfumu, n’kumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa inatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi+ mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene anali kukhala ku Damasiko.+ Inawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti: 19 “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Taona, ndakutumizira mphatso+ ya siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke kwa ine.”+ 20 Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga mizinda ya Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka,+ ndi Kinereti yense mpaka dziko lonse la Nafitali.+ 21 Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama+ ndipo anapitiriza kukhala ku Tiriza.+ 22 Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse,+ moti palibe amene sanaitanidwe, ndipo iwo anatenga miyala ya ku Rama ndi matabwa ake, zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa inatenga zinthu zimenezo n’kuyamba kukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini, ndi mzinda wa Mizipa.+

23 Nkhani zina zonse zokhudza Asa, ndi zochita zake zonse zamphamvu, ndiponso zonse zimene anachita, ndi mizinda imene anamanga, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. Koma mu ukalamba wake,+ mapazi ake anachita matenda.+ 24 Pomalizira pake, Asa anagona ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake.+ Ndiyeno Yehosafati+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

25 Nadabu+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli m’chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli kwa zaka ziwiri. 26 Iye anali kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova, ndipo anapitiriza kutsatira njira ya bambo ake+ ndi machimo awo amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 27 Ndiyeno Basa+ mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anayamba kuchitira chiwembu Nadabu. Iye anapha Nadabu kumzinda wa Gebetoni,+ womwe unali m’manja mwa Afilisiti, pa nthawi imene Nadabu ndi Aisiraeli onse anali kuukira Gebetoni. 28 Choncho Basa anapha Nadabu m’chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 29 Basa atangokhala mfumu, anapha anthu onse a m’nyumba ya Yerobowamu. Sanasiye wa m’banja la Yerobowamu aliyense ali ndi moyo kufikira atawatha onse, malinga ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Ahiya Msilo.+ 30 Izi zinachitika chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita,+ ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli, komanso chifukwa cha zinthu zokwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli zimene Yerobowamu anachita.+ 31 Nkhani zina zokhudza Nadabu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 32 Pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo masiku awo onse.+

33 M’chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Basa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Isiraeli yense ku Tiriza kwa zaka 24.+ 34 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndiponso anapitiriza kuyenda m’njira ya Yerobowamu+ ndi m’tchimo lake limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+

16 Tsopano mawu a Yehova otsutsana ndi Basa anafikira Yehu+ mwana wa Haneni,+ kuti: 2 “Ngakhale kuti ndinakukweza kukuchotsa kufumbi+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli,+ iwe wayenda m’njira ya Yerobowamu+ n’kuchimwitsa anthu anga Aisiraeli mwa kundikwiyitsa ndi machimo awo.+ 3 Tsopano ine ndidzaseseratu Basa ndi nyumba yake, ndipo ndidzachititsa nyumba yake kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 4 Munthu aliyense wa m’banja la Basa amene adzafere mumzinda, agalu adzamudya ndipo amene adzafere kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya.”+

5 Nkhani zina zokhudza Basa ndi zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 6 Pomalizira pake, Basa anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda ku Tiriza.+ Kenako Ela mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 7 Mawu a Yehova otsutsana ndi Basa ndi nyumba yake+ anafikira Yehu mwana wa Haneni mneneri. Mawuwo anali otsutsana naye chifukwa cha zoipa zonse zimene Basayo anachita pamaso pa Yehova mwa kumukwiyitsa+ ndi ntchito ya manja ake,+ ndiponso chifukwa chakuti iye anapha+ Nadabu. Mawuwo anali akuti nyumba yake idzakhala ngati nyumba ya Yerobowamu.

8 M’chaka cha 26 cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa anakhala mfumu ya Isiraeli ku Tiriza kwa zaka ziwiri. 9 Kenako mtumiki wake Zimiri,+ mkulu woyang’anira hafu ya magaleta, anayamba kum’konzera chiwembu. Anam’konzera chiwembucho pamene Ela anali kumwa+ mowa mpaka kuledzera kunyumba+ ya Ariza ku Tiriza. Ariza anali woyang’anira banja la mfumu ku Tirizako. 10 Ndiyeno Zimiri anafika n’kukantha+ Ela mpaka kumupha, ndipo iye anayamba kulamulira m’malo mwake. Zimenezi zinachitika m’chaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. 11 Iye atangokhala pampando wachifumu n’kuyamba kulamulira, anapha anthu onse a m’nyumba ya Basa. Sanasiye ndi moyo munthu aliyense wokodzera khoma+ wa m’banja la Basa kapena abale ake amene akanatha kubwezera magazi ake,+ kapenanso anzake. 12 Choncho Zimiri anafafaniza nyumba yonse ya Basa,+ malinga ndi mawu a Yehova+ otsutsana ndi Basa amene analankhula kudzera mwa Yehu mneneri.+ 13 Anawafafaniza chifukwa cha machimo onse a Basa ndi machimo amene Ela+ mwana wake anachita, ndiponso chifukwa cha machimo amene anachimwitsa nawo Aisiraeli. Iwo anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 14 Nkhani zina zokhudza Ela ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

15 M’chaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anakhala mfumu ku Tiriza kwa masiku 7.+ Pa nthawiyo anthu anali atamanga msasa pafupi ndi mzinda wa Gebetoni,+ umene unali wa Afilisiti, kuti authire nkhondo. 16 Patapita nthawi, anthu mumsasawo anamva kuti: “Zimiri wachitira chiwembu mfumu ndipo waipha.” Choncho tsiku limenelo, Aisiraeli onse omwe anali kumsasako anaveka ufumu Omuri,+ mkulu wa asilikali, kuti akhale mfumu ya Isiraeli. 17 Kenako Omuri ndi Aisiraeli onse amene anali naye, anachoka ku Gebetoni n’kupita kukaukira+ mzinda wa Tiriza. 18 Zimiri atangoona kuti mzindawo walandidwa, anakalowa munsanja yomwe inali panyumba ya mfumu n’kuyatsa nyumbayo iye ali mkati mwake, moti anafera momwemo.+ 19 Anafa chifukwa cha machimo ake amene anachita mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndiponso mwa kuyenda m’njira ya Yerobowamu ndi m’tchimo limene iyeyo anachita mwa kuchimwitsa Isiraeli.+ 20 Nkhani zina zokhudza Zimiri ndi chiwembu chimene anakonza, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

21 Pa nthawi imeneyi m’pamene anthu a ku Isiraeli anayamba kugawikana m’magulu awiri.+ Gulu limodzi linayamba kutsatira Tibini mwana wa Ginati kuti amuveke ufumu, ndipo gulu linalo linayamba kutsatira Omuri. 22 Pomalizira pake, anthu amene anali kutsatira Omuri anagonjetsa otsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa, ndipo Omuri anayamba kulamulira.

23 M’chaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli ndipo analamulira zaka 12. Ku Tiriza analamulirako zaka 6. 24 Kenako anagula phiri la Samariya* kwa Semeri ndi matalente* awiri a siliva. Ndiyeno anayamba kumanga mzinda paphiripo n’kuutcha dzina la Semeri mbuye wa phirilo, loti Samariya.+ 25 Omuri anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anachita zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.+ 26 Iye anali kuyenda m’njira zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati,+ ndi m’tchimo lake limene anachimwitsa nalo Isiraeli mwa kukwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 27 Nkhani zina zokhudza Omuri, zimene anachita ndi zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 28 Pomalizira pake Omuri anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anamuika m’manda ku Samariya. Kenako Ahabu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

29 Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli m’chaka cha 38 cha Asa mfumu ya Yuda. Iye analamulira Isiraeli ku Samariya+ zaka 22. 30 Ahabu mwana wa Omuri anachita zoipa kwambiri pamaso pa Yehova kuposa onse amene anakhalapo iye asanakhale.+ 31 Komanso, ngati kuti kuyenda m’machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati inali nkhani yaing’ono,+ Ahabu anakwatira+ Yezebeli+ mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni,+ ndipo anayamba kukatumikira Baala+ ndi kum’gwadira. 32 Kuwonjezera apo, anamanga guwa lansembe la Baala m’kachisi+ wa Baala amene iye anamanga ku Samariya. 33 Ahabu anaimikanso mzati wopatulika,+ ndipo iye anachita zinthu zambiri zokwiyitsa+ Yehova Mulungu wa Isiraeli kuposa mafumu onse a Isiraeli amene anakhalapo iye asanakhale.

34 M’masiku ake, Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko. Atangoyala maziko ake, Abiramu mwana wake woyamba anafa, ndipo atangoika zitseko zake za pachipata, Segubu mwana wake wotsiriza anafa. Izi zinachitika mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.+

17 Eliya+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi+ analankhula ndi Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli+ amene ndimam’tumikira,+ sikugwa mame kapena mvula+ zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.”+

2 Kenako mawu+ a Yehova anafika kwa iye, akuti: 3 “Choka kuno, lowera chakum’mawa ukabisale+ m’chigwa* cha Keriti, chimene chili kum’mawa kwa Yorodano. 4 Uzikamwa+ madzi mumtsinje umene uli m’chigwacho, ndipo ndidzalamula akhwangwala+ kuti azikakupatsa chakudya.”+ 5 Nthawi yomweyo, Eliya anachita mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ Anapita kukakhala m’mphepete mwa chigwa cha Keriti chimene chili kum’mawa kwa Yorodano. 6 Akhwangwala ankamubweretsera mkate ndi nyama m’mawa ndi madzulo, ndipo iye ankamwa madzi mumtsinje umene unali m’chigwacho.+ 7 Koma patapita masiku angapo, mtsinjewo unauma,+ chifukwa padziko lapansi sipanabwere mvula.

8 Tsopano mawu a Yehova anafika kwa iye, akuti:+ 9 “Nyamuka, upite ku Zarefati+ m’dziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wina wa kumeneko, mkazi wamasiye, kuti azikakupatsa chakudya.” 10 Chotero Eliya ananyamuka kupita ku Zarefati n’kulowa pachipata cha mzindawo. Kenako anaona mayi, mkazi wamasiye, akutola nkhuni. Ndiyeno anamuitana n’kumuuza kuti: “Undipatseko madzi pang’ono m’chikho kuti ndimwe.”+ 11 Atanyamuka kuti akatenge madziwo, anamuitananso n’kumuuza kuti: “Undibweretserekonso mkate pang’ono+ m’manja mwako.” 12 Atamva zimenezi mayiyo anati: “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo,+ ndilibe mkate,+ koma ufa pang’ono+ mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono+ mumtsuko waung’ono. Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.”+

13 Ndiyeno Eliya anamuuza kuti: “Usachite mantha.+ Pita ukachite mogwirizana ndi mawu ako. Koma pa zimene uli nazozo, ukayambe wandikonzera mtanda waung’ono wa mkate,+ n’kubwera nawo kwa ine. Kenako, ukakonze chakudya chako ndi cha mwana wako. 14 Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu siutha, ndipo mafuta amene ali mumtsuko waung’ono saatha, kufikira tsiku limene Yehova adzagwetse mvula padziko lapansi.’”+ 15 Choncho mayiyo anapita n’kukachita monga mmene Eliya ananenera. Ndipo iye, banja lake, ndi Eliya anadya kwa masiku ambiri.+ 16 Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe,+ ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya.

17 Pambuyo pa zimenezi, mwana wamwamuna wa mayi wa m’nyumbamo, anadwala. Matenda ake anakula kwambiri mpaka anamwalira.+ 18 Mayiyo ataona zimenezi, anauza Eliya kuti: “Ndili nanu chiyani+ inu munthu wa Mulungu woona? Mwabwera kwa ine kudzandikumbutsa cholakwa changa+ ndi kudzapha mwana wanga.” 19 Koma Eliya anauza mayiyo kuti: “Bweretsa kuno mwana wakoyo.” Ndiyeno anatenga mwanayo m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kuchipinda chapadenga.+ Chipinda chimenechi n’chimene Eliya anali kukhalamo, ndipo anagoneka mwanayo pabedi lake.+ 20 Atatero, anayamba kufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga,+ kodi mukuchitiranso zoipa mkazi wamasiye amene ndikukhala naye monga mlendo wake, mwa kupha mwana wake?” 21 Ndiyeno anakumbatira mwanayo+ katatu ali pabedipo n’kufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo+ wa mwanayu ubwerere mwa iye.” 22 Kenako Yehova anamva mawu a Eliya,+ moti moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye, ndipo anakhala wamoyo.+ 23 Tsopano Eliya anatenga mwanayo n’kutsika naye kuchokera kuchipinda chapadenga chija, n’kumupereka kwa mayi ake. Ndiyeno anati: “Taona, mwana wako ali moyo.”+ 24 Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”+

18 Patapita masiku ambiri,+ mawu a Yehova anafikira Eliya m’chaka chachitatu, kuti: “Pita ukaonekere kwa Ahabu, chifukwa ndikufuna kubweretsa mvula padziko lapansi.”+ 2 Chotero Eliya anapita kukaonekera kwa Ahabu. Pa nthawiyi n’kuti njala itafika poipa kwambiri+ ku Samariya.

3 Pa nthawi imeneyo Ahabu anaitana Obadiya, yemwe anali woyang’anira banja la Ahabuyo.+ (Obadiya anali atasonyeza kuti anali munthu woopa Yehova kwambiri.+ 4 Choncho pamene Yezebeli+ anapha aneneri a Yehova,+ Obadiya anatenga aneneri 100 n’kuwagawa m’magulu awiri, gulu lililonse aneneri 50. Atatero anakawabisa kuphanga ndipo anali kuwapatsa mkate ndi madzi.)+ 5 Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita m’dzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira+ woti tidyetse mahatchi ndi nyulu, kuti nyamazi zisapitirize kufa.”+ 6 Choncho anagawana koti aliyense alowere. Ahabu analowera njira ina, Obadiyanso analowera njira ina.+

7 Obadiya akuyenda, anangoona Eliya akubwera kudzakumana naye.+ Nthawi yomweyo anamuzindikira ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Kodi ndinu mbuyanga+ Eliya?” 8 Iye anamuyankha kuti: “Ndinedi. Pita ukanene kwa mbuye wako kuti,+ ‘Eliya wabwera.’” 9 Koma Obadiya anati: “Kodi ndachita tchimo lanji+ kuti mupereke mtumiki wanune m’manja mwa Ahabu kuti andiphe? 10 Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo,+ palibe mtundu kapena ufumu kumene mbuye wanga sanatumize anthu kuti akakufunefuneni. Akanena kuti, ‘Kuno kulibe,’ ankauza ufumuwo ndi mtunduwo kuti ulumbire kuti walephera kukupezani.+ 11 Kodi tsopano mukundiuza kuti, ‘Pita ukanene kwa mbuye wako kuti: “Eliya wabwera”’? 12 Zimene zichitike n’zakuti ine ndikasiyana nanu, mzimu+ wa Yehova ubwera n’kukutengani kupita nanu kwina kumene ine sindikukudziwa. Ineyo ndikhala nditamuuza kale Ahabu, koma iyeyo sadzakupezani choncho adzandipha ndithu.+ Komatu mtumiki wanune ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ubwana wanga.+ 13 Kodi mbuye wanga simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli anapha aneneri a Yehova? Ndinabisa aneneri 100 a Yehova m’phanga.+ Ndinawagawa m’magulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse, ndipo ndinali kuwapatsa mkate ndi madzi.+ 14 Kodi tsopano mukunena kuti, ‘Pita, ukanene kwa mbuye wako kuti: “Eliya wabwera”’? Ndithu akandipha.”+ 15 Koma Eliya anati: “Pali Yehova wa makamu,+ Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira, lero ndionekera kwa Ahabu.”

16 Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu n’kumuuza zimenezi. Ndiyeno Ahabuyo anapita kukakumana ndi Eliya.

17 Ahabu atangomuona Eliya, anati: “Ndiwe eti! Iwe ndiwe munthu amene wachititsa kuti Isiraeli anyanyalidwe.”+

18 Eliya anayankha kuti: “Ine sindinachititse kuti Isiraeli anyanyalidwe,+ koma inu ndi nyumba ya bambo anu ndi amene mwachititsa kuti anyanyalidwe,+ chifukwa anthu inu munasiya kutsatira malamulo a Yehova+ n’kuyamba kutsatira Abaala.+ 19 Tsopano tumizani uthenga ndipo musonkhanitse Aisiraeli onse kwa ine paphiri la Karimeli.+ Musonkhanitsenso aneneri 450 a Baala+ ndi aneneri 400 a mzati wopatulika,+ amene amadya patebulo la Yezebeli.”+ 20 Choncho Ahabu anatumiza uthenga kwa ana onse a Isiraeli, n’kusonkhanitsanso aneneri+ paphiri la Karimeli.

21 Kenako Eliya anayandikira anthu onsewo n’kunena kuti: “Kodi mukayikakayika* mpaka liti?+ Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni,+ koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo.” Koma anthuwo sanamuyankhe chilichonse. 22 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Ndilipo ndekha mneneri wa Yehova amene watsala,+ ndekhandekha basi, koma aneneri a Baala alipo 450. 23 Tsopano iwowo apeze ng’ombe zamphongo ziwiri zing’onozing’ono. Asankhepo ng’ombe imodzi n’kuiduladula. Ndiyeno aiike pankhuni koma asayatsepo moto. Ineyo ndikonza ng’ombe inayo n’kuiika pankhuni, koma sindiyatsapo moto. 24 Kenako muitane dzina la mulungu wanu.+ Inenso ndiitana dzina la Yehova, ndipo Mulungu amene ayankhe potumiza moto+ ndiye Mulungu woona.”+ Anthu onsewo atamva zimenezi anayankha kuti: “Zili bwino.”

25 Tsopano Eliya anauza aneneri a Baala kuti: “Yambani ndinu kusankha ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi ndi kuikonza, chifukwa mulipo ambiri. Muitane dzina la mulungu wanu koma musayatse moto.” 26 Choncho anatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo imene Eliya anawapatsa, n’kuikonza. Kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira m’mawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse,+ ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha ngati akuvina, kuzungulira guwa lansembe limene anamanga. 27 Pofika masana Eliya anayamba kuwaseka+ ndipo anali kunena kuti: “Muitaneni mokuwa kwambiri chifukwa iye ndi mulungu.+ Mwina watanganidwa ndi zinazake, kapena wapita kuchimbudzi.+ Mwinanso wagona, ndipo muyenera kum’dzutsa.”+ 28 Iwo anayamba kuitana mokuwa kwambiri n’kumadzicheka+ ndi mipeni ndi mikondo ing’onoing’ono malinga ndi mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kutuluka ndi kuyenderera pamatupi awo. 29 Iwo anapitiriza kuchita ngati aneneri+ mpaka dzuwa linapendeka. Anapitirizabe mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu, koma sipanamveke mawu alionse. Palibe anawayankha kapena kuwamvera.+

30 Patapita nthawi, Eliya anauza anthu onsewo kuti: “Bwerani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo anabweradi. Kenako iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linagumuka.+ 31 Choncho Eliya anatenga miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Yakobo, yemwe mawu a Yehova anam’fikira,+ akuti: “Dzina lako lidzakhala Isiraeli.”+ 32 Ndi miyalayo, Eliya anamanga guwa lansembe+ kuti dzina la Yehova+ lilemekezedwe. Anakumbanso ngalande kuzungulira guwa lansembe lonselo. Ngalandeyo kukula kwake inali ngati malo amene angafesepo mbewu zokwana miyezo iwiri ya seya.* 33 Kenako anayalapo nkhuni,+ ndipo anaduladula ng’ombe yaing’ono yamphongo ija, n’kuiika pamwamba pa nkhunizo. Tsopano iye anati: “Tungani madzi odzaza mitsuko inayi ikuluikulu. Muwathire pansembe yopserezayo ndiponso pankhunizo.” 34 Kenako iye anati: “Thiraninso madzi ena.” Anthuwo anathiranso. Ndiyeno Eliya anati: “Thiraninso kachitatu.” Choncho anthuwo anathiranso kachitatu. 35 Chotero madziwo anayenderera pansi ponse paguwa lansembelo. Iye anathiranso madzi m’ngalande muja mpaka kudzaza.

36 Pa nthawi+ yopereka nsembe yambewu, Eliya mneneri anayandikira guwa lansembelo n’kunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Isiraeli,+ lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli,+ ndi kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+ 37 Ndiyankheni Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe kuti inu Yehova+ ndinu Mulungu woona, ndiponso kuti mwabweza mitima yawo.”+

38 Atatero, moto+ wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopsereza+ ija, nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.+ 39 Anthu onsewo ataona zimenezo, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo ananena kuti: “Yehova ndiye Mulungu woona! Yehova ndiye Mulungu woona!” 40 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Gwirani aneneri a Baala! Muonetsetse kuti pasapezeke wothawa!” Nthawi yomweyo anawagwira, ndipo Eliya anatsetserekera nawo kuchigwa cha Kisoni,+ n’kukawapha kumeneko.+

41 Tsopano Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa,+ chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.”+ 42 Ahabu anapitadi kukadya ndi kukamwa. Koma Eliya anapita pamwamba pa phiri la Karimeli. Ndiyeno anakhala chogwada+ ataika nkhope yake pakati pa mawondo ake.+ 43 Kenako anauza mtumiki wake kuti: “Pita ukayang’ane mbali ya kunyanja.” Mtumikiyo anapita n’kukayang’anadi, ndiyeno anati: “Kulibe kalikonse.” Koma Eliya anamubweza n’kumuuza kuti, “Pita ukayang’anenso.” Anachita zimenezi mpaka maulendo 7.+ 44 Pa ulendo wa 7, mtumikiyo anati: “Taonani! Kuli kamtambo kakang’ono ngati chikhatho cha dzanja la munthu, ndipo kakukwera m’mwamba kuchokera m’nyanja.”+ Tsopano Eliya anauza mtumiki wakeyo kuti: “Pita ukauze Ahabu kuti, ‘Mangirirani mahatchi kugaleta,+ ndipo tsetserekani kuti chimvula chisakutsekerezeni.’” 45 Pa nthawiyo kumwamba kunachita mdima wa mitambo ndipo kunja kunawomba mphepo.+ Kenako kunayamba kugwa chimvula chambiri.+ Ahabu anali akuyenda pagaleta mpaka anakafika ku Yezereeli.+ 46 Dzanja la Yehova linali ndi Eliya,+ moti iye anakokera chovala chake m’chiuno n’kuchimanga,+ ndipo anayamba kuthamanga n’kupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.+

19 Kenako Ahabu+ anauza Yezebeli+ zonse zimene Eliya anachita, ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.+ 2 Yezebeli atamva zimenezo, anatuma munthu kwa Eliya kuti akamuuze kuti: “Milungu yanga indilange+ mowirikiza,+ ngati pofika nthawi ino mawa sindidzachititsa moyo wako kukhala ngati moyo wa aliyense wa aneneriwo.” 3 Choncho Eliya anachita mantha moti ananyamuka n’kuyamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake,+ mpaka anakafika ku Beere-seba+ wa ku Yuda.+ Mtumiki wake anamusiya kumeneko, 4 ndipo iyeyo analowa m’chipululu n’kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake,+ ndipo anakhala pansi pake. Ndiyeno anayamba kupempha kuti afe, ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga+ Yehova, pakuti sindine woposa makolo anga.”

5 Kenako anagona pansi mpaka tulo tinam’peza pansi pa kamtengo kaja.+ Tsopano kunabwera mngelo+ amene anamukhudza,+ n’kumuuza kuti: “Dzuka udye.” 6 Atayang’ana, anaona kuti kumutu kwake kuli chikho cha madzi ndi mkate wozungulira+ uli pamiyala yotentha. Ndipo Eliya anayamba kudya ndi kumwa, kenako anagonanso. 7 Patapita kanthawi, mngelo+ wa Yehova uja anabweranso kachiwiri n’kumukhudza, ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye, popeza ulendowu wakukulira.”+ 8 Choncho anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anatha kuyenda masiku 40,+ usana ndi usiku, mpaka kukafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.+

9 Atafika kumeneko, analowa m’phanga+ kuti usiku agone mmenemo. Kenako anamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?”+ 10 Iye anayankha kuti: “Ndachitira nsanje kwambiri+ inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe,+ ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha.+ Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.”+ 11 Koma Mulungu anati: “Tuluka, kaime paphiri pamaso pa Yehova.”+ Kenako Yehova anadutsa,+ ndipo kunawomba chimphepo champhamvu chomwe chinali kung’amba mapiri ndi kuphwanya matanthwe pamaso pa Yehova.+ (Yehova sanali mumphepoyo.) Pambuyo pa chimphepocho, kunachita chivomezi.+ (Yehova sanali m’chivomezicho.) 12 Pambuyo pa chivomezicho, kunabuka moto.+ (Yehova sanali m’motowo.) Pambuyo pa motowo, panamveka mawu achifatse apansipansi.+ 13 Eliya atangomva mawuwo, nthawi yomweyo anaphimba nkhope yake ndi chovala chake,+ ndipo anatuluka kukaima pakhomo la phangalo. Pamenepo panamveka mawu olankhula naye, ndipo mawuwo anam’funsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?”+ 14 Iye anayankha kuti: “Ndachitira nsanje kwambiri inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.”+

15 Kenako Yehova anamuuza kuti: “Nyamuka, bwerera udzere kuchipululu cha Damasiko.+ Pita ukadzoze+ Hazaeli+ kuti akhale mfumu ya Siriya. 16 Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi+ kuti akhale mfumu ya Isiraeli, ndipo Elisa+ mwana wa Safati wa ku Abele-mehola,+ ukam’dzoze kuti akhale mneneri m’malo mwa iwe.+ 17 Zomwe zidzachitike n’zakuti, wothawa lupanga la Hazaeli,+ adzaphedwa ndi Yehu,+ ndipo wothawa lupanga la Yehu, adzaphedwa ndi Elisa.+ 18 Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala,+ ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.”+

19 Chotero Eliya anachoka kumeneko n’kupita kwa Elisa mwana wa Safati, ndipo anam’peza akulima ndi pulawo+ yokokedwa ndi ng’ombe ziwiri zamphongo. Panali mapulawo 12 oterowo ndipo pulawo yake inali kumbuyo kwa onsewo. Choncho Eliya anapita pamene panali Elisa n’kumuponyera chovala chake chauneneri.+ 20 Zitatero, Elisa anasiya ng’ombe zamphongozo n’kuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikapsompsone kaye bambo anga ndi mayi anga,+ kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.” 21 Choncho anabwerera n’kutenga ng’ombe zamphongo ziwiri n’kuzipha.*+ Anatenga mitengo ya pulawo+ ya ng’ombezo n’kuphikira nyama yake. Kenako anaipereka kwa anthu kuti adye. Atatero, iye ananyamuka n’kutsatira Eliya ndipo anayamba kum’tumikira.+

20 Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya anasonkhanitsa gulu lake lonse lankhondo ndiponso mahatchi+ ndi magaleta.+ Atatero ananyamuka pamodzi ndi mafumu ena 32,+ n’kupita kukazungulira+ mzinda wa Samariya+ kuti amenyane nawo. 2 Kenako anatumiza amithenga+ kumzindawo, kwa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti akamuuze kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, 3 ‘Siliva ndi golide wako akhala wanga, ndipo akazi ako ndi ana ako aamuna ooneka bwino kwambiri, akhala anga.’”+ 4 Pamenepo mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mogwirizana ndi mawu anu mbuyanga mfumu, ine ndi zanga zonse tili m’manja mwanu.”+

5 Pambuyo pake amithenga aja anabweranso n’kudzanena kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, ‘Ndinakutumizira uthenga wonena kuti, “Undipatse siliva wako, golide wako, akazi ako, ndi ana ako aamuna. 6 Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatumiza atumiki anga kwa iwe. Iwo adzafufuza paliponse m’nyumba mwako ndi m’nyumba za atumiki ako, ndipo adzatenga chilichonse chamtengo wapatali+ kwa iwe.”’”

7 Mfumu ya Isiraeli itamva mawu amenewa, inaitanitsa akulu onse a m’dzikolo+ n’kuwauza kuti: “Taonani, munthu uyu akufuna kutibweretsera tsoka.+ Ananditumizira uthenga woti akufuna akazi anga, ana anga aamuna, siliva wanga, ndi golide wanga, ndipo ine sindinamukanize ayi.” 8 Pamenepo, akulu onse ndi anthu onse anauza mfumuyo kuti: “Musamvere zimenezo, ndipo musagwirizane nazo.” 9 Choncho Ahabu anauza amithenga a Beni-hadadi kuti: “Mukauze mbuyanga mfumu kuti, ‘Zonse zimene munandiuza poyamba paja, ine mtumiki wanu ndichita. Koma zimene mwanena kachiwirizi, sindingathe kuchita.’” Atumiki a Beni-hadadi aja atamva zimenezi, ananyamuka kukapereka uthengawo kwa mfumu yawo.

10 Tsopano Beni-hadadi anatumizira Ahabu uthenga wakuti: “Milungu+ yanga indilange mowirikiza,+ ngati fumbi la ku Samariya lidzakwanire kuti anthu onse onditsatira atape lodzaza manja.”+ 11 Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Amuna inu mukamuuze kuti, ‘Musayambe kudzitama nkhondo isanayambe ngati kuti mwapambana kale nkhondoyo.’”+ 12 Beni-hadadi atangomva mawu amenewa, pamene iye ndi mafumu amene anali naye anali kumwa mowa+ m’misasa, anauza antchito ake kuti: “Konzekerani nkhondo!” Choncho iwo anayamba kukonzekera kukachita nkhondo ndi mzindawo.

13 Ndiyeno mneneri wina anapita kwa Ahabu mfumu ya Isiraeli,+ n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Kodi waona khamu lalikulu lonseli? Ndilipereka m’manja mwako lero, ndipo udziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 14 Ahabu anafunsa kuti: “Kudzera mwa ndani?” Mneneriyo anayankha kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kudzera mwa anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo.’” Pomalizira Ahabu anafunsa kuti: “Ndani akayambitse nkhondoyo?” Mneneriyo anayankha kuti: “Inuyo!”

15 Ahabu anawerenga anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo, ndipo anakwana 232.+ Atatha kuwerenga amenewa, anawerenga asilikali onse a ana a Isiraeli, omwe anakwana 7,000. 16 Iwo ananyamuka masana pamene Beni-hadadi anali kumwa ndi kuledzera+ m’misasa, pamodzi ndi mafumu ena 32 amene anali kumuthandiza aja. 17 Anyamata+ otumikira akalonga oyang’anira zigawo ndiwo anatsogolera. Iwo atangofika, Beni-hadadi anatumizako anthu ndipo anabwera kudzamuuza kuti: “Kwabwera anthu ochokera ku Samariya.” 18 Iye atamva anati: “Agwireni amoyo, kaya abwerera mtendere kapena abwerera nkhondo.”+ 19 Anali kunena za anyamata otumikira akalonga oyang’anira zigawo, amene anabwera kuchokera kumzinda pamodzi ndi gulu lankhondo limene linali m’mbuyo mwawo. 20 Kenako aliyense anayamba kupha mdani wake. Asiriyawo+ anayamba kuthawa+ ndipo Aisiraeli anawathamangitsa. Koma Beni-hadadi mfumu ya Siriya anathawa atakwera hatchi, pamodzi ndi amuna ena okwera pamahatchi. 21 Mfumu ya Isiraeli inawatsatira n’kumapha mahatchi ndi kuwononga magaleta+ awo, ndipo inapha Asiriya ochuluka zedi.

22 Pambuyo pake mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Pitani, kalimbitseni gulu lanu lankhondo+ ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ popeza kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya ija idzabweranso kudzamenyana nanu.”+

23 Atumiki a mfumu ya Siriya anauza mfumu yawo kuti: “Mulungu wawo ndi Mulungu wa mapiri.+ N’chifukwa chake anatiposa mphamvu, choncho tiyeni tikamenyane nawo m’chigwa tione ngati sitiwaposa mphamvu. 24 Tsopano muchite izi: Muchotse mafumu onse+ pa maudindo awo ndipo muike abwanamkubwa m’malo mwawo.+ 25 Inuyo musonkhanitse gulu lankhondo, chiwerengero chake chofanana ndi gulu limene linagonja lija. Chiwerengero cha mahatchi ndi magaleta chikhalenso chofanana ndi choyamba chija, ndipo tipite tikamenyane nawo m’chigwa kuti tikaone ngati sitikawaposa mphamvu.”+ Choncho mfumuyo inamvera mawu awo n’kuchitadi zimenezo.

26 Kumayambiriro kwa chaka, Beni-hadadi anasonkhanitsa Asiriya+ n’kupita ku Afeki+ kuti akamenyane ndi Aisiraeli. 27 Ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kutenga zonse zofunikira+ ndipo ananyamuka kupita kukakumana nawo. Ana a Isiraeliwo anamanga msasa kutsogolo kwa Asiriya. Iwo anali ngati timagulu tiwiri ting’onoting’ono ta mbuzi pamene Asiriyawo anadzaza dziko lonse.+ 28 Kenako munthu wa Mulungu woona+ uja anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza Asiriya anena kuti: “Yehova ndi Mulungu wa mapiri, osati Mulungu wa zigwa,” ndipereka khamu lalikulu lonseli m’manja mwako,+ ndipo anthu inu mudziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+

29 Magulu awiriwa anakhala moyang’anizana m’misasa masiku 7.+ Pa tsiku la 7 nkhondo inayambika, ndipo ana a Isiraeli anapha asilikali oyenda pansi a Asiriya okwanira 100,000 tsiku limodzi. 30 Anthu amene anatsala anathawira kumzinda wa Afeki,+ ndipo khoma linagwera amuna 27,000 amene anatsala.+ Beni-hadadi anathawa+ ndipo pomalizira pake anafika mumzindawo n’kulowa m’chipinda chamkati.+

31 Ndiyeno atumiki ake anamuuza kuti: “Tamva kuti mafumu a nyumba ya Isiraeli ndiwo mafumu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha.+ Tiyeni tivale ziguduli*+ m’chiuno mwathu+ ndi kumanga zingwe kumutu kwathu, kuti tipite kwa mfumu ya Isiraeli. Mwina sikakuphani.”+ 32 Choncho anavala ziguduli m’chiuno n’kumanga zingwe kumutu kwawo. Atatero anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kunena kuti: “Kapolo wanu Beni-hadadi wati, ‘Chonde musandiphe.’” Ahabu anati: “Kodi akadali ndi moyo? Amene uja ndi m’bale wanga.” 33 Choncho anthuwo+ anaona kuti chimenechi ndi chizindikiro choti zinthu zikhala bwino, ndipo atangomva zimenezi, anaona kuti mfumuyo ikunenadi zochokera mumtima mwake. Kenako anati: “Beni-hadadi ndi m’bale wanu.” Ahabu atamva zimenezi anati: “Pitani mukam’tenge.” Choncho Beni-hadadi anabwera kwa Ahabu ndipo nthawi yomweyo Ahabu anauza anthu kuti akweze Beni-hadadi m’galeta.+

34 Tsopano Beni-hadadi anauza Ahabu kuti: “Ndibweza mizinda+ imene bambo anga analanda bambo anu, ndipo inuyo mutenga misewu ku Damasiko mofanana ndi mmene bambo anga anatengera misewu ku Samariya.”

Ahabu anayankha kuti: “Tikapanga pangano+ loti udzachitadi zimenezi, ndikusiya kuti uzipita kwanu.”

Atatero anachita naye pangano ndipo anamuuza kuti azipita kwawo.

35 Munthu wina wochokera pakati pa ana a aneneri,*+ pomvera mawu+ a Yehova anauza mnzake kuti: “Ndimenye!” Koma mnzakeyo anakana kum’menya. 36 Choncho mneneriyo anauza mnzakeyo kuti: “Popeza sunamvere mawu a Yehova, ukachoka pano ukumana ndi mkango ndipo ukupha ndithu.” Kenako mnzakeyo anachoka ndipo mkango+ unamupeza n’kumupha.+

37 Ndiyeno anapita kwa munthu wina n’kumuuza kuti: “Ndimenye!” Munthuyo anam’menyadi mpaka kumuvulaza.

38 Kenako, mneneriyo anakaima m’mphepete mwa msewu n’kumakadikirira mfumu ija, atadzimanga kansalu kumaso kuti asadziwike.+ 39 Pamene mfumu inali kudutsa, mneneriyo analankhula mofuula kwa mfumuyo kuti:+ “Ine mtumiki wanu ndinapita pakatikati pa nkhondo. Munthu wina yemwe anali kuchoka kunkhondoko anandisungitsa munthu n’kundiuza kuti, ‘Uyang’anire munthu uyu. Akangosowa, moyo wako+ ulowa m’malo mwa moyo wake,+ apo ayi ulipira siliva wolemera talente* imodzi.’+ 40 Koma mtumiki wanune nditatanganidwa ndi zina, munthu uja anasowa.” Pamenepo mfumu ya Isiraeliyo inamuuza kuti: “Chiweruzo chako n’chomwecho. Wagamula wekha.”+ 41 Mfumuyo itangonena zimenezi, mneneriyo anachotsa msangamsanga kansalu kamene kanali kumaso kwake kaja, ndipo mfumu ya Isiraeliyo inamuzindikira kuti anali mmodzi wa aneneri.+ 42 Tsopano mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza wamasula munthu woyenera kuwonongedwa ndi ine,+ moyo wako ulowa m’malo mwake+ ndipo anthu ako alowa m’malo mwa anthu ake.’”+ 43 Mfumu ya Isiraeliyo itamva zimenezi, inanyamuka n’kumapita kunyumba kwake ili yachisoni ndi yokhumudwa,+ ndipo inafika ku Samariya.+

21 Ndiyeno panali munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli, umene unali ku Yezereeli,+ pafupi ndi nyumba yachifumu ya Ahabu mfumu ya Samariya. 2 Ahabu anauza Naboti kuti: “Ndipatse+ munda wako wa mpesawu+ kuti ukhale munda+ wanga woti ndizilimamo masamba,+ chifukwa uli pafupi ndi nyumba yanga. M’malo mwa munda wakowu ndikupatsa munda wina wa mpesa, wabwino kuposa umenewu. Ngati ungafune,+ ndiugula ndi ndalama.” 3 Koma Naboti anayankha Ahabu kuti: “Sindingachite zimenezo+ pamaso pa Yehova,+ kupereka cholowa cha makolo anga kwa inuyo.”+ 4 Choncho Ahabu analowa m’nyumba mwake ali wachisoni ndi wokhumudwa chifukwa cha mawu amene Naboti Myezereeli anamuuza, onena kuti: “Sindikupatsani cholowa cha makolo anga.” Ndiyeno anakagona pabedi lake n’kutembenukira kukhoma,+ ndipo sanadye chakudya.

5 Kenako Yezebeli+ mkazi wake anabwera n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simukusangalala+ komanso simukudya chakudya?” 6 Ahabu anamuyankha kuti: “N’chifukwa chakuti ndinalankhula ndi Naboti Myezereeli kuti, ‘Ndigulitse munda wako wa mpesa. Kapena ngati ukufuna, ndikupatsa munda wina wa mpesa m’malo mwa umenewu.’ Koma anandiyankha kuti, ‘Sindikupatsani munda wanga wa mpesa.’”+ 7 Ndiyeno Yezebeli mkazi wake anamuuza kuti: “Kodi muziwalamulira chonchi Aisiraeliwa?+ Dzukani, idyani chakudya, mtima wanu usangalale. Ineyo ndikupatsani munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli.”+ 8 Choncho Yezebeli analemba makalata+ m’dzina la Ahabu n’kuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzinda umodzi ndi Naboti. 9 M’makalatamo analembamo kuti:+ “Uzani anthu kuti asale kudya, ndipo muike Naboti patsogolo pa anthu onse. 10 Ndiyeno mupeze anthu awiri+ opanda pake+ adzakhale patsogolo pake ndi kupereka umboni wotsutsana naye.+ Adzanene kuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndi mfumu!’+ Kenako mukamutulutse kunja ndi kum’ponya miyala kuti afe.”+

11 Choncho amuna a mumzinda wake, akulu ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzindawo, anachita zimene Yezebeli anawatuma, mogwirizana ndi zimene iye analemba m’makalata amene anawatumizira.+ 12 Iwo anauza anthu kuti asale kudya+ ndipo anauza Naboti kuti akhale patsogolo pa anthuwo. 13 Kenako amuna awiri opanda pake anabwera n’kukhala patsogolo pa Naboti. Ndiyeno amuna opanda pakewo anayamba kupereka umboni wotsutsana ndi Naboti pamaso pa anthuwo, wakuti: “Naboti watemberera Mulungu ndi mfumu!”+ Pambuyo pake anamutulutsira kunja kwa mzindawo n’kumuponya miyala mpaka anafa.+ 14 Atatero anatumiza uthenga kwa Yezebeli, wakuti: “Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa.”+

15 Yezebeli atangomva kuti Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa, nthawi yomweyo anauza Ahabu kuti: “Nyamukani, katengeni munda wa mpesa wa Naboti Myezereeli+ umene anakana kukugulitsani uja, popeza Naboti salinso moyo koma wafa.” 16 Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, nthawi yomweyo ananyamuka n’kupita kumunda wa mpesa wa Naboti Myezereeli, kukautenga kuti ukhale wake.+

17 Tsopano mawu a Yehova+ anafikira Eliya+ wa ku Tisibe, kuti: 18 “Nyamuka, pita ku Samariya+ ukakumane ndi Ahabu mfumu ya Isiraeli. Iye ali m’munda wa mpesa wa Naboti, ndipo wapita kumeneko kukautenga kuti ukhale wake. 19 Ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi wapha munthu+ n’kutenganso munda wake?”’+ Ukamuuzenso kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pamalo+ amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako, a iweyo.”’”+

20 Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. ‘Popeza watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+ 21 ndikubweretsera tsoka+ ndipo ndithu ndidzaseseratu nyumba yako,+ ndi kupha munthu aliyense wokodzera khoma+ wa m’banja la Ahabu, ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake mu Isiraeli. 22 Ndithu ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa n’kuchimwitsanso Isiraeli.’+ 23 Komanso ponena za Yezebeli, Yehova wanena kuti, ‘Agalu adzamudya Yezebeli m’munda wa ku Yezereeli.+ 24 Munthu wa m’banja la Ahabu wofera mumzinda, agalu adzamudya, ndipo wofera kuthengo, mbalame zam’mlengalenga zidzamudya.+ 25 Palibenso munthu wina wofanana ndi Ahabu.+ Iye anadzipereka kuti achite zoipa pamaso pa Yehova ndiponso mkazi wake Yezebeli+ anamulimbikitsa+ kuchita zimenezo. 26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri mwa kutsatira mafano onyansa+ monga momwe Aamori, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, anachitira.’”+

27 Ahabu atangomva mawu amenewa, anang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo anali kuyenda mwachisoni.+ 28 Ndiyeno mawu a Yehova anafikira Eliya wa ku Tisibe, kuti: 29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Popeza wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake.+ M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.”+

22 Kwa zaka zitatu, panalibe nkhondo pakati pa Siriya ndi Isiraeli. 2 M’chaka chachitatucho, Yehosafati+ mfumu ya Yuda inapita kwa mfumu ya Isiraeli. 3 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda m’manja mwa mfumu ya Siriya.” 4 Kenako inafunsa Yehosafati kuti: “Kodi upita nane kunkhondo ku Ramoti-giliyadi?”+ Yehosafati anayankha mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu ako ndi amodzi.+ Mahatchi anga n’chimodzimodzi ndi mahatchi ako.”

5 Komabe Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, umve kaye mawu a Yehova.”+ 6 Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri pamodzi.+ Analipo amuna pafupifupi 400, ndipo inawafunsa kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena ndisapite?” Iwo anayankha kuti: “Pitani,+ ndipo Yehova akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”

7 Koma Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene watsala? Ngati alipo, tiyeni tifunsire kwa Mulungu kudzera mwa ameneyo.”+ 8 Poyankha, mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye,+ koma ineyo ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa.+ Munthuyo dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Musalankhule choncho mfumu.”+

9 Chotero mfumu ya Isiraeli inaitana nduna ina ya panyumba ya mfumu,+ n’kuiuza kuti: “Kaitane Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye msangamsanga.”+ 10 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anali atakhala pabwalo* la pachipata cha Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu.+ Pamaso pawo panali aneneri onse ndipo anali kuchita zinthu monga mmene aneneri amachitira.+ 11 Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Ndi nyanga izi mudzakankha Asiriya mpaka kuwatha.’”+ 12 Aneneri ena onse analinso kulosera zofanana ndi zomwezo, ndipo anali kunena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana. Yehova akaperekadi mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+

13 Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Tamvera, mawu amene aneneri onse alankhula kwa mfumu ndi abwino. Nawenso mawu ako akakhale ngati mawu a mmodzi wa iwo, ndipo ukalankhule zabwino.”+ 14 Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Yehova anene kwa ine n’zimene ndikalankhule.”+ 15 Kenako anafika kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana. Mosakayikira, Yehova akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+ 16 Ndiyeno mfumuyo inamuuza kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzilankhula kwa ine zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?”+ 17 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika+ m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+

18 Mfumu ya Isiraeli itamva zimenezi inauza Yehosafati kuti: “Pajatu ndinakuuza kuti, ‘Adzalosera zoipa za ine, osati zabwino.’”+

19 Mikaya anapitiriza kunena kuti: “Choncho imvani mawu a Yehova:+ Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu,+ makamu onse akumwamba ataimirira kudzanja lake lamanja ndi kumanzere kwake.+ 20 Kenako Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu, kuti apite ku Ramoti-giliyadi n’kukafa?’ Choncho uyu anayamba kunena zakutizakuti, uyunso n’kumanena zakutizakuti.+ 21 Pomalizira pake, mzimu wina+ unabwera kudzaima pamaso pa Yehova n’kunena kuti, ‘Ine ndikam’pusitsa.’ Ndipo Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukam’pusitsa motani?’+ 22 Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukam’pusitsadi ndipo zikakuyendera bwino.+ Pita kachite momwemo.’+ 23 Choncho Yehova waika mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anu onsewa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+

24 Tsopano Zedekiya mwana wa Kenaana anayandikira Mikaya ndipo anam’menya mbama,+ n’kunena kuti: “Kodi mzimu wa Yehova wachoka bwanji kwa ine n’kukalankhula ndi iwe?”+ 25 Pamenepo Mikaya anati: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe m’chipinda chamkati+ kukabisala.”+ 26 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Tengani Mikaya mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu.+ 27 Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti:+ “Kam’tsekereni munthu uyu.+ Muzim’patsa chakudya chochepa+ ndi madzinso ochepa, kufikira ine nditabwerera mu mtendere.”’”+ 28 Pamenepo Mikaya ananena kuti: “Mukakabwereradi mu mtendere, ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Anatinso: “Imvani anthu nonsenu.”+

29 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 30 Tsopano mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike, ndipo ndimenya nawo nkhondo.+ Koma iweyo uvale zovala zako zachifumu.”+ Chotero mfumu ya Isiraeli inadzisintha+ n’kuyamba kumenya nawo nkhondo.+ 31 Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu ake 32+ oyang’anira asilikali okwera magaleta, kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamng’ono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.”+ 32 Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Ndithu iyi ndiyo mfumu ya Isiraeli.”+ Choncho anatembenuka kuti amenyane naye, koma Yehosafati anayamba kukuwa popempha thandizo.+ 33 Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, nthawi yomweyo anasiya kum’thamangitsa ndi kubwerera.+

34 Ndiyeno munthu wina anakoka uta n’kuponya muvi wake chiponyeponye, koma analasa mfumu ya Isiraeli pampata umene unali pakati pa chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo, ndi zovala zake zina zodzitetezera. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti:+ “Tembenuza dzanja lako ndipo unditulutse m’bwalo lankhondoli, chifukwa ndavulala kwambiri.” 35 Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo, ndipo mfumuyo anaiimiritsa m’galeta moyang’anizana ndi Asiriya. Potsirizira pake inafa+ madzulo, ndipo magazi ochokera pachilonda chake anali kuyenderera mkati mwa galeta lankhondolo.+ 36 Kenako, dzuwa litatsala pang’ono kulowa, mumsasamo munamveka mfuu yaikulu, yakuti: “Aliyense azipita kumzinda wake, ndi kudziko lake!”+ 37 Chotero mfumuyo inafa. Ataibweretsa ku Samariya, anaiika m’manda ku Samariyako.+ 38 Kenako anayamba kutsuka galeta lankhondolo padziwe la ku Samariya ndipo agalu anayamba kunyambita magazi a mfumuyo,+ mogwirizana ndi mawu amene Yehova ananena.+ (Mahule ankasambanso padziwe limeneli.)

39 Nkhani zina zokhudza Ahabu ndi zochita zake zonse, komanso nyumba yaminyanga ya njovu+ imene anamanga, ndi mizinda yonse imene anamanga, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 40 Pomalizira pake Ahabu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Ahaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

41 Yehosafati+ mwana wa Asa anakhala mfumu ya Yuda m’chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya Isiraeli. 42 Yehosafati anali ndi zaka 35 pamene anayamba kulamulira. Iye analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili. 43 Yehosafati anayenda m’njira zonse za Asa bambo ake. Sanapatuke panjirazo, ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka. Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+ 44 Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya Isiraeli.+ 45 Nkhani zina zokhudza Yehosafati ndi zochita zake zamphamvu ndiponso momwe anamenyera nkhondo, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 46 Mahule aamuna a pakachisi+ amene anatsalira m’masiku a Asa bambo ake, Yehosafati anawachotsa m’dzikolo.+

47 Pa nthawi imeneyo ku Edomu+ kunalibe mfumu. Nduna ndi imene inali kulamulira monga mfumu.+

48 Yehosafati anapanga zombo za ku Tarisi+ kuti zizipita ku Ofiri kukatenga golide, koma sizinapite chifukwa zinasweka ku Ezioni-geberi.+ 49 Panali pa nthawi imeneyo pamene Ahaziya mwana wa Ahabu anapempha Yehosafati kuti: “Bwanji antchito anga apite pamodzi ndi antchito anu m’zombozo?” Koma Yehosafati anakana.+

50 Pomalizira pake, Yehosafati anagona ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide+ kholo lake. Kenako Yehoramu+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

51 Ahaziya+ mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya m’chaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 52 Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova. Anayenda m’njira ya bambo ake,+ m’njira ya mayi ake,+ ndiponso m’njira ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Isiraeli.+ 53 Ahaziya anapitiriza kutumikira Baala+ ndi kum’gwadira, ndipo anapitiriza kukwiyitsa+ Yehova Mulungu wa Isiraeli, malinga ndi zonse zimene bambo ake anachita.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Kapena kuti “Ame” m’Chiheberi.

Kapena kuti “zikumbutso; zilimbikitso.”

Mawu ake enieni, “m’choonadi.”

Onani Zakumapeto 5.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Eze 45:14.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Mf 4:22.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Mawu ake enieni, “kachisi,” mwina kutanthauza Malo Oyera.

Kapena kuti “kutsindwi.”

Mwina umenewu unali mtengo wa mtundu wa paini.

Onani Zakumapeto 13.

Kapena “zipinda” kapenanso “mitengo yapamwamba pa nsanamira.” M’Chiheberi anangoti “15.”

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Mawu ake enieni, “nyanja yosungunula.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani Zakumapeto 12.

M’Malemba achiheberi mulibe nambala yake.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

Palembali mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “n’kulumbiritsa” akunena za lumbiro limene munthu ankatha kulandira nalo chilango ngati analumbira zonama.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kapena kuti “Dziko Lopanda Pake,” kapenanso “Dziko Lomangidwa Maunyolo.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.

Onani Zakumapeto 12.

Golide ameneyu angakwane ndalama pafupifupi madola 256,643,000 a ku America.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.

Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Pa 2Mb 11:20, 21, akutchedwa Abisalomu.

Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu akuti “Samariya” akutanthauza kuti “la Fuko la Semeri.”

Onani Zakumapeto 12.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake enieni, “mudumphiradumphira maganizo awiri osiyana.”

Onani Zakumapeto 12.

Mawu ake enieni, “n’kuzipereka nsembe.”

Ena amati “masaka.”

Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena bungwe la aneneri.

Onani Zakumapeto 12.

Mawu ake enieni, “popunthira mbewu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena