Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Psalms 1:1-150:6
  • Masalimo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masalimo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Masalimo

Masalimo*

BUKU LOYAMBA

(Masalimo 1 – 41)

1 Wodala+ ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,+

Saima m’njira ya anthu ochimwa,+

Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+

 2 Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+

Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+

 3 Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi,+

Umene umabala zipatso m’nyengo yake,+

Umenenso masamba ake safota,+

Ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.+

 4 Koma oipa sali choncho.

Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.+

 5 N’chifukwa chake oipa adzatsutsidwa pa chiweruzo,+

Ndipo ochimwa sadzapezeka pagulu la olungama.+

 6 Pakuti Yehova amadziwa njira za olungama,+

Koma oipa adzatheratu pamodzi ndi njira zawo.+

2 N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe,+

Ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikung’ung’udza za chinthu chopanda pake?+

 2 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,+

Ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana.+

Atero kuti alimbane ndi Yehova+ komanso wodzozedwa wake.+

 3 Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,+

Ndipo titaye zingwe zawo kutali ndi ife!”+

 4 Iye wokhala kumwamba+ adzaseka,

Yehova adzawanyodola.+

 5 Pa nthawiyo, adzawalankhula mu mkwiyo wake,+

Adzawasokoneza ataipidwa kwambiri.+

 6 Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+

Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+

 7 Ndinene za lamulo la Yehova.

Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+

Lero, ine ndakhala bambo ako.+

 8 Tandipempha,+ ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako,+

Ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.+

 9 Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+

Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+

10 Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira,

Lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweruza a dziko lapansi.+

11 Tumikirani Yehova mwamantha.+

Kondwerani ndipo nthunthumirani.+

12 Psompsonani mwanayo+ kuopera kuti Mulungu angakwiye,

Ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo.+

Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumira.+

Odala ndi onse amene akuthawira kwa iye.+

Nyimbo ya Davide pamene anali kuthawa mwana wake Abisalomu.+

3 Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere?+

N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka?+

 2 Ponena za moyo wanga, ambiri akuti:

“Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.”+ [Seʹlah.*]

 3 Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+

Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+

 4 Ndidzafuulira Yehova mokweza,

Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.]

 5 Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo.

Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.+

 6 Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumi

Amene andiukira ndi kundizungulira.+

 7 Nyamukani,+ inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!+

Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano.+

Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.+

 8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+

Madalitso anu ali pa anthu anu.+ [Seʹlah.]

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe.+ Nyimbo ya Davide.

4 Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama.+

M’masautso anga mundiimiritse pamalo otakasuka.

Mundikomere mtima+ ndipo imvani pemphero langa.

 2 Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza chifukwa cha ulemerero wanga+ kufikira liti?

Mudzakonda zinthu zopanda pake kufikira liti?

Mudzafunafuna nkhani yoti mundinamizire kufikira liti? [Seʹlah.]

 3 Choncho dziwani kuti Yehova adzapatula wokhulupirika wake.+

Yehova adzamva ndikaitana.+

 4 Ngati mwakwiya, musachimwe.+

Lankhulani mumtima mwanu, muli pabedi panu,+ ndipo mukhale chete. [Seʹlah.]

 5 Perekani nsembe zachilungamo,+

Ndipo khulupirirani Yehova.+

 6 Pali ambiri amene akunena kuti: “Ndani adzationetsa zinthu zabwino?”

Inu Yehova, tiunikeni ndi kuwala kwa nkhope yanu.+

 7 Mudzasangalatsadi mtima wanga,+

Kuposanso mmene iwo amasangalalira, mbewu ndi vinyo wawo watsopano zikachuluka.+

 8 Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere,+

Pakuti inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Nehiloti.* Nyimbo ya Davide.

5 Mvetserani mawu anga+ inu Yehova,

Mumvetse kudandaula kwanga.

 2 Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo,+

Inu Mfumu yanga+ ndi Mulungu wanga, chifukwa ndimapemphera kwa inu.+

 3 Inu Yehova, m’mawa mudzamva mawu anga,+

M’mawa ndidzalankhula nanu ndipo ndidzadikira yankho.+

 4 Pakuti inu sindinu Mulungu wokondwera ndi zoipa,+

Palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu ngakhale kwa kanthawi kochepa.+

 5 Palibe anthu odzitama amene angaime pamaso panu.+

Mumadana ndi onse ochita zopweteka ena.+

 6 Mudzawononga olankhula bodza.+

Munthu wokhetsa magazi+ ndi wachinyengo,+ Yehova amaipidwa naye.

 7 Koma ine ndidzalowa m’nyumba yanu+

Chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

Ndidzawerama nditayang’ana kumene kuli kachisi wanu wopatulika chifukwa chokuopani.+

 8 Inu Yehova, nditsogolereni m’chilungamo chanu+ chifukwa adani anga andizungulira.+

Salazani njira yanu kuti ndiyendemo popanda chopunthwitsa.+

 9 Pakuti m’kamwa mwawo simutuluka mawu okhulupirika.+

Mitima yawo yadzaza ndi zinthu zoipa.+

Mmero wawo ndi manda otseguka.+

Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.+

10 Mulungu adzawapeza ndi mlandu.+

Adzagwa ndi ziwembu zawo zomwe.+

Muwamwaze chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,+

Chifukwa iwo akupandukirani.+

11 Koma onse othawira kwa inu adzakondwa.+

Adzafuula mokondwera mpaka kalekale.*+

Ndipo inu mudzawateteza.

Okonda dzina lanu adzakondwa chifukwa cha inu.+

12 Pakuti inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.+

Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu+ ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe chapansipansi* ndi zoimbira za zingwe.+ Nyimbo ya Davide.

6 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya.+

Musandiwongolere mutapsa mtima.+

 2 Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+

Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.

 3 Moyo wanga wasokonezeka kwambiri.+

Kodi inu Yehova, mudzadikira kufikira liti?+

 4 Bwererani+ mudzapulumutse moyo wanga, inu Yehova.+

Ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+

 5 Pakuti akufa satchula za inu.+

Kodi ndani angatamande inu ali m’Manda?*+

 6 Ndalefuka chifukwa cha kuusa moyo* kwanga.+

Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.+

Ndimakhathamitsa bedi langa ndi misozi.+

 7 Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+

Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+

 8 Ndichokereni pamaso panga inu nonse ochita zopweteka ena,+

Chifukwa Yehova adzamva ndithu mawu a kulira kwanga.+

 9 Yehova adzamva ndithu pempho langa loti andikomere mtima.+

Yehova adzalandira pemphero langa.+

10 Adani anga onse adzachita manyazi kwambiri+ ndipo adzasokonezeka.

Adzabwerera, ndipo nthawi yomweyo adzachita manyazi.+

Nyimbo yoimba polira* imene Davide anaimbira Yehova, yonena za mawu a Kusi M’benjamini.

7 Inu Yehova Mulungu wanga,+ ine ndathawira kwa inu.+

Ndipulumutseni kwa onse ondizunza ndipo mundilanditse,+

 2 Kuti pasapezeke wondikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+

Pasapezeke wondikwatula popanda wondilanditsa.+

 3 Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita cholakwa chilichonse,+

Ngati manja anga achita zosalungama zilizonse,+

 4 Ngati munthu wondichitira zabwino ndamubwezera zoipa,+

Kapena ngati ndafunkha zinthu za aliyense wondichitira zoipa amene sanaphule kanthu,+

 5 Mdani wanga afunefune moyo wanga,+

Ndipo aupeze ndi kuupondaponda pafumbi.

Ulemerero wanga aukwirire m’fumbi. [Seʹlah.]

 6 Nyamukani, inu Yehova, mu mkwiyo wanu.+

Imirirani ndi kukhaulitsa amene andisonyeza mkwiyo ndi kundichitira zoipa.+

Dzukani ndi kundithandiza,+ pakuti mwalamula kuti chiweruzo chiperekedwe.+

 7 Mitundu ya anthu isonkhane ndi kukuzungulirani,

Ndipo inu mubwerere kumwamba ndi kuwakhaulitsa.

 8 Yehova adzapereka chigamulo ku mitundu ya anthu.+

Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa,+

Komanso mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+

 9 Chonde, thetsani kuipa kwa anthu oipa,+

Ndipo khazikitsani wolungama.+

Mulungu pokhala wolungama+ akuyesa mtima+ ndi impso.+

10 Chishango changa chili ndi Mulungu,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+

11 Mulungu ndi Woweruza wolungama,+

Ndipo Mulungu amapereka ziweruzo tsiku lililonse.

12 Ngati munthu sadzabwerera kusiya zoipa,+ Mulungu adzanola lupanga lake,+

Adzakunga uta wake ndi kukonzekera kulasa.+

13 Iye adzadzikonzera zida za imfa,+

Ndipo adzapanga mivi yake kukhala yoyaka moto walawilawi.+

14 Taonani! Wina ali ndi pakati pa zinthu zoipa,+

Watenga pakati pa mavuto ndipo ndithu adzabereka chinyengo.+

15 Iye wafukula dzenje, walikumbadi.+

Koma adzagwera m’dzenje lokumba yekha.+

16 Mavuto ake adzabwerera pamutu pake,+

Ndipo chiwawa chake chidzatsikira paliwombo pake.+

17 Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha chilungamo chake.+

Ndidzaimba nyimbo motsatizana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina+ la Yehova Wam’mwambamwamba.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ya Davide.

8 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,+

Inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!+

 2 M’kamwa mwa ana aang’ono ndi ana oyamwa mwakhazikitsamo zamphamvu,+

Chifukwa cha amene akukuchitirani zoipa.+

Mwatero kuti mugonjetse mdani wanu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa.+

 3 Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu,+

Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+

 4 Ndimaganiza kuti: Munthu+ ndani kuti muzimuganizira,+

Ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?+

 5 Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu,*+

Kenako munamuveka ulemerero+ ndi ulemu monga chisoti chachifumu.+

 6 Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+

Mwaika zonse pansi pa mapazi ake:+

 7 Nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, zonse zimenezi,+

Komanso zilombo zakutchire.+

 8 Mbalame zam’mlengalenga ndi nsomba za m’nyanja,+

Chilichonse choyenda m’njira za pansi pa nyanja.+

 9 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide.

א [ʼAʹleph]

9 Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.+

Ndidzalengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+

 2 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,+

Ndidzaimba nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+

ב [Behth]

 3 Adani anga akabweranso,+

Adzapunthwa ndi kuwonongeka pamaso panu,+

 4 Chifukwa mwandiweruzira mlandu wanga ndi dandaulo langa.+

Mwakhala pampando wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+

ג [Giʹmel]

 5 Mwadzudzula anthu a mitundu ina,+ mwawononga oipa.+

Dzina lawo mwalifafaniza mpaka kalekale, mwalifafaniza mpaka muyaya.+

 6 Kusakaza kwa mdani kwatheratu tsopano,+

Mizinda imene mwaifafaniza, nayonso yatheratu.+

Dzina la mdani wanu silidzatchulidwanso.+

ה [Heʼ]

 7 Koma Yehova adzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale,+

Adzakhazikitsa mpando wake wachifumu kuti aweruze.+

 8 Iye adzaweruza anthu padziko lapansi mwachilungamo.+

Adzazenga mlandu mitundu ya anthu moyenerera.+

ו [Waw]

 9 Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa,+

Adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.+

10 Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani,+

Pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.+

ז [Zaʹyin]

11 Anthu inu, imbani nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda Yehova amene akukhala m’Ziyoni.+

Fotokozani ntchito zake kwa mitundu ya anthu.+

12 Pofunafuna okhetsa magazi,+ iye adzakumbukira ndithu anthu osautsidwa.+

Sadzaiwala ndithu kulira kwawo.+

ח [Chehth]

13 Ndikomereni mtima inu Yehova. Onani mmene anthu odana nane akundisautsira,+

Inu Mulungu amene mukundinyamula kundichotsa pazipata za imfa.+

14 Ndichitireni zimenezi kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zotamandika+

Pazipata+ za mwana wamkazi wa Ziyoni,+

Kuti ndikondwere ndi chipulumutso chanu.+

ט [Tehth]

15 Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+

Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+

16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+

Woipa wakodwa mumsampha wa ntchito ya manja ake.+

Higayoni.* [Seʹlah.]

י [Yohdh]

17 Anthu oipa+ adzapita ku Manda,+

Ngakhalenso anthu onse a mitundu ina amene aiwala Mulungu.+

18 Pakuti waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse,+

Ndiponso chiyembekezo cha ofatsa sichidzatha konse.+

כ [Kaph]

19 Nyamukani, inu Yehova! Munthu asakuposeni mphamvu.+

Anthu a mitundu ina aweruzidwe pamaso panu.+

20 Ikani mantha m’mitima yawo, inu Yehova,+

Kuti anthu a mitundu ina adziwe kuti iwo ndi anthu ochokera kufumbi.+ [Seʹlah.]

ל [Laʹmedh]

10 N’chifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?+

N’chifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya masautso?+

 2 Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+

Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+

 3 Pakuti woipa amadzitamandira ndi zilakolako zake zadyera,+

Ndipo wopanga phindu lachinyengo+ amadzitamanda.

נ [Nun]

Iye amanyoza Yehova.+

 4 Chifukwa cha kutukumuka mtima kwake, woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.+

Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+

 5 Zochita zake zimayenda bwino nthawi zonse.+

Zigamulo zanu zili pamwamba kwambiri pamene iye sangathe kuziona.+

Onse omuchitira zoipa amawanyodola.+

 6 Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.+

Palibe chimene chidzandichitikira ku mibadwomibadwo.”+

פ [Peʼ]

 7 M’kamwa mwake mwadzaza matemberero, chinyengo ndi kupondereza ena.+

Pansi pa lilime lake pamatuluka mavuto ndi zopweteka ena.+

 8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.

Amabisalira munthu wosalakwa ndi kumupha.+

ע [ʽAʹyin]

Maso ake amafunafuna waumphawi.+

 9 Amadikirira anthu pamalo obisika ngati mkango pamalo ake obisalapo.+

Amawadikirira+ kuti atenge mokakamiza munthu wosautsika.

Amakulunga wosautsika mu ukonde wake ndi kumutenga mokakamiza.+

10 Wosautsikayo amaponderezedwa, amawerama ndi chisoni,

Ndipo khamu la anthu achisoni limagwera m’manja amphamvu a woipayo.+

11 Mumtima mwake+ amanena kuti: “Mulungu waiwala zochita zanga.+

Wabisa nkhope yake.+

Ndithudi, sadzaona kalikonse.”+

ק [Qohph]

12 Nyamukani,+ inu Yehova. Inu Mulungu, tukulani dzanja lanu.+

Musaiwale anthu osautsika.+

13 N’chifukwa chiyani woipa amanyoza Mulungu?+

Mumtima mwake amati: “Simudzandiimba mlandu.”+

ר [Rehsh]

14 Inu mwaona mavuto ndi masautso.

Mumawayang’anabe kuti muchitepo kanthu.+

Waumphawi,+ mwana wamasiye,* amadziikiza m’manja mwanu.

Inu mwakhala mthandizi wake.+

ש [Shin]

15 Thyolani dzanja la woipa ndi wankhanzayo.+

Fufuzani zoipa zake zonse ndi kumulanga kufikira zoipazo zitatha.+

16 Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

Mitundu yatheratu padziko lapansi.+

ת [Taw]

17 Mudzamva kuchonderera kwa anthu ofatsa,+ inu Yehova.

Mudzakonzekeretsa mitima yawo.+

Mudzatchera khutu lanu,+

18 Kuti muweruze mwana wamasiye komanso woponderezedwa.+

Mudzatero kuti munthu wamba wochokera kufumbi asachititsenso anthu ena kunjenjemera.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

11 Ine ndathawira kwa Yehova.+

Kodi mulibe mantha? Mukundiuza kuti:

“Thawirani kumapiri anu ngati mbalame!+

 2 Pakuti oipa akunga uta,+

Akonzekeretsa mivi yawo kuti aiponye ndi uta,

Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.+

 3 Kodi munthu wolungama angachite chiyani

Maziko achilungamo atagumulidwa?”+

 4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+

Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+

Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.

 5 Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe,+

Ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.+

 6 Iye adzavumbitsira oipa misampha, moto ndi sulufule,+

Komanso mphepo yotentha, monga gawo limene ayenera kumwa.+

 7 Pakuti Yehova ndi wolungama.+ Amakonda ntchito zolungama.+

Anthu owongoka mtima ndi amene adzaona nkhope yake.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe chapansipansi.*+ Nyimbo ya Davide.

12 Ndipulumutseni,+ inu Yehova, pakuti anthu okhulupirika atha.+

Anthu okhulupirika atheratu pakati pa ana a anthu.

 2 Iwo amalankhulana zabodza.+

Amalankhulana ndi milomo yoshashalika+ komanso ndi mitima iwiri.+

 3 Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengo

Ndi lilime lolankhula modzikuza.+

 4 Iye adzadula anthu onena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.+

Timalankhula chilichonse chimene tikufuna ndi milomo yathu. Ndani angatilamulire?”

 5 Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+

Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+

Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+

 6 Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+

Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka.

 7 Inu Yehova mudzawayang’anira.+

Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku m’badwo uwu mpaka kalekale.

 8 Anthu oipa akuyendayenda ponseponse,

Chifukwa ana a anthu amayamikira zoipa.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

13 Kodi mudzandiiwala kufikira liti, inu Yehova?+ Mpaka muyaya?+

Mudzandibisira nkhope yanu kufikira liti?+

 2 Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti?

Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?

Kodi mdani wanga adzadzikweza pamaso panga kufikira liti?+

 3 Ndiyang’aneni. Ndiyankheni, inu Yehova Mulungu wanga.

Walitsani maso anga+ kuti ndisagone mu imfa.+

 4 Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!”

Kutinso adani anga asakondwere chifukwa chakuti ine ndadzandira.+

 5 Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.+

Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.+

 6 Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

14 Wopusa amanena mumtima mwake kuti:

“Kulibe Yehova.”+

Anthu oterewa amachita zoipa,+ ndipo amachita zinthu zonyansa.

Palibe amene akuchita zabwino.+

 2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+

Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+

 3 Onse apatuka,+ ndipo onsewo ndi achinyengo.+

Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+

Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+

 4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+

Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+

Iwo sanaitane pa Yehova.+

 5 Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+

Pakuti Yehova ali pakati pa khamu* la anthu olungama.+

 6 Anthu inu mumanyazitsa malangizo a munthu wosautsika,

Chifukwa Yehova ndiye pothawirapo pake.+

 7 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+

Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+

Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

Nyimbo ya Davide.

15 Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?+

Ndani angakhale m’phiri lanu lopatulika?+

 2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,+ amene amachita chilungamo,+

Ndi kulankhula zoona mumtima mwake.+

 3 Iye sanena miseche ndi lilime lake.+

Sachitira mnzake choipa,+

Ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.+

 4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+

Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+

Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+

 5 Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+

Mikitamu* ya Davide.

16 Ndisungeni, inu Mulungu, pakuti ndathawira kwa inu.+

 2 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Ubwino wanga sungakupindulitseni,+

 3 Koma ungapindulitse oyera amene ali padziko lapansi.

Anthu aulemerero amenewo, ndi amene ndimakondwera nawo.”+

 4 Zopweteka zimachuluka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangira.+

Ine sindidzatsanula nsembe zawo zachakumwa zothira magazi,+

Ndipo sindidzatchula dzina lawo ndi milomo yanga.+

 5 Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa,+ komanso chikho changa.+

Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa.

 6 Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.+

Ndithudi, gawo limene ndapatsidwa ndalivomereza.

 7 Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+

Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.+

 8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+

Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.+

 9 Choncho moyo wanga ukukondwera, ndipo ndidzakhala wosangalala.+

Komanso ndidzakhala wotetezeka.+

10 Pakuti simudzasiya moyo wanga m’Manda.+

Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.+

11 Mudzandidziwitsa njira ya moyo.+

Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira.+

Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.+

Pemphero la Davide.

17 Imvani dandaulo lolungama, inu Yehova. Mvetserani kulira kwanga kochonderera.+

Tcherani khutu ku pemphero langa limene likutuluka pamilomo yopanda chinyengo.+

 2 Chiweruzo changa chichokere kwa inu.+

Maso anu aone kuwongoka mtima kwanga.+

 3 Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+

Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+

Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+

 4 Kunena za ntchito za anthu,

Ndakhala wosamala mwa kusunga mawu a pakamwa panu, kuti ndisatengere njira ya wachifwamba.+

 5 Mapazi anga ayendebe m’njira zanu,+

Mmene sadzapunthwa ngakhale pang’ono.+

 6 Ine ndikuitana pa inu, chifukwa mudzandiyankha, inu Mulungu.+

Tcherani khutu kwa ine. Imvani mawu anga.+

 7 Sonyezani kukoma mtima kosatha mwa kuchita zodabwitsa,+ inu Mpulumutsi wa anthu othawira kwa inu,

Amene akuthawa anthu ogalukira dzanja lanu lamanja.+

 8 Ndisungeni monga mwana wa diso,+

Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu,+

 9 Chifukwa cha anthu oipa amene akundipondereza.

Adani a moyo wanga atsala pang’ono kundipeza.+

10 Mitima yawo siimva chisoni,*+

Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.+

11 Tsopano adaniwo atizungulira, kulikonse kumene tingapite.+

Akutiyang’anitsitsa kuti atigwetse.+

12 Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+

Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.

13 Nyamukani, inu Yehova, yang’anizanani naye maso ndi maso woipayo.+

M’gonjetseni. Pulumutsani moyo wanga kwa woipayo ndi lupanga lanu.+

14 Ndipulumutseni kwa anthu ndi dzanja lanu, inu Yehova,+

Ndipulumutseni kwa anthu a m’nthawi* ino,+ amene gawo lawo lili m’moyo uno.+

Anthu amene mimba zawo mwazidzaza ndi chuma chanu chobisika,+

Amene ali ndi ana aamuna ochuluka,+

Ndipo amakundikira ana awo chuma.+

15 Koma ine ndidzaona nkhope yanu m’chilungamo.+

Podzuka, ndidzakhutira pokuonani.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati:

18 Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+

 2 Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+

Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+

Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+

 3 Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+

Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+

 4 Zingwe za imfa zinandikulunga,+

Chikhamu cha anthu opanda pake chinali kundiopseza.+

 5 Zingwe za Manda zinandizungulira.+

Ndinayang’anizana ndi misampha ya imfa.+

 6 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,

Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+

Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+

Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+

 7 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+

Maziko a mapiri anagwedezeka,+

Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+

 8 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+

Makala onyeka anatuluka mwa iye.

 9 Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+

Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake.

10 Iye anafika atakwera pakerubi wouluka.+

Mulungu anali kuuluka mwaliwiro pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+

11 Kenako anapanga mdima kukhala malo ake obisalamo,+

Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda,

Zimene zinamuzungulira ngati msasa wake.+

12 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka mitambo yake,+

Munatulukanso matalala ndi makala onyeka a moto.+

13 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+

Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake,+

Anatulutsanso matalala ndi makala onyeka a moto.

14 Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+

Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+

15 Ndipo ngalande za pansi pa madzi zinaonekera,+

Maziko a dziko lapansi anakhala poonekera.+

Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwanu.+

16 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+

Anandivuula m’madzi akuya.+

17 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+

Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+

18 Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+

Koma Yehova anandichirikiza.+

19 Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+

Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+

20 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+

Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+

Sindinachoke kwa Mulungu wanga. Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.+

22 Zigamulo zake zonse zili pamaso panga,+

Ndipo malamulo ake sindidzawataya.+

23 Ndidzakhalabe wopanda cholakwa pamaso pake,+

Ndipo ndidzayesetsa kupewa kuchita cholakwa.+

24 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+

Andibwezere mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.+

25 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+

Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+

26 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+

Kwa munthu wopotoka maganizo mudzadzisonyeza kuti ndinu wochenjera,+

27 Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+

Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+

28 Pakuti inu Yehova mudzandiyatsira nyale yanga,+

Mulungu wanga adzandiunikira mu mdima.+

29 Pakuti ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba.+

Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+

30 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+

Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+

Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+

31 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+

Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+

32 Mulungu woona Ndiye amandilimbitsa,*+

Ndipo adzasalaza njira yanga.+

33 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+

Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+

34 Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+

Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+

35 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+

Dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza,+

Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.+

36 Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga,+

Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+

37 Ndidzathamangitsa adani anga ndi kuwapeza,

Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+

38 Ndidzawaphwanya zibenthuzibenthu kuti asadzukenso.+

Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+

39 Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.

Mudzakomola ondiukira.+

40 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+

Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+

41 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+

Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+

42 Ndidzawapera kukhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.+

Ndidzawakhuthula ngati matope a mumsewu.+

43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+

Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+

Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+

44 Anthu akangomva mphekesera chabe zokhudza ine, adzandimvera.+

Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+

45 Alendo adzatha mphamvu,

Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+

46 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+

Mulungu wa chipulumutso changa akhale wokwezeka.+

47 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga.+

Iye amagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika kunsi kwa mapazi anga.+

48 Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.+

Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+

Mudzandilanditsa kwa munthu wachiwawa.+

49 N’chifukwa chake ndidzakutamandani, inu Yehova pakati pa mitundu.+

Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+

50 Iye akuchita ntchito zazikulu za chipulumutso kwa mfumu yake,+

Ndipo akusonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+

kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

19 Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+

Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+

 2 Tsiku lililonse limanena mawu,+

Ndipo usiku uliwonse umasonyeza nzeru.+

 3 Sizilankhula, kapena kutulutsa mawu.

Mawu awo samveka.+

 4 Zingwe zawo zoyezera zafika padziko lonse lapansi,+

Mawu awo amveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+

Kumwambako Mulungu wamangira dzuwa hema.+

 5 Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka m’chipinda chake,+

Limakondwa ngati mmene mwamuna wamphamvu amachitira akamathamanga m’njira.+

 6 Limatuluka kuchokera kumalekezero ena a kumwamba,

Ndi kuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+

Palibe chinthu chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.+

 7 Chilamulo+ cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa moyo.+

Zikumbutso+ za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+

 8 Malamulo+ ochokera kwa Yehova ndi olungama,+ amasangalatsa mtima.+

Chilamulo+ cha Yehova ndi choyera,+ chimatsegula maso.+

 9 Kuopa+ Yehova n’koyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.

Zigamulo+ za Yehova n’zolondola,+ ndipo pa mbali iliyonse zasonyezadi kuti ndi zolungama.+

10 N’zolakalakika kuposa golide, kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+

N’zotsekemera* kuposa uchi,+ inde kuposa uchi umene ukukha m’zisa.+

11 Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+

Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+

12 Ndani angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+

Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.+

13 Komanso mundiletse kuchita modzikuza, ine mtumiki wanu.+

Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+

Pamenepo ndidzakhala wopanda chifukwa,+

Ndipo ndidzakhalabe wopanda milandu yambiri yophwanya malamulo.

14 Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga,+

Zikukondweretseni, inu Yehova, Thanthwe langa+ ndi Wondiwombola.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

20 Yehova akuyankheni pa tsiku la nsautso.+

Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+

 2 Atumize thandizo kuchokera kumalo oyera.+

Akuchirikizeni ali ku Ziyoni.+

 3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.+

Alandire mafuta a nsembe zanu zopsereza.+ [Seʹlah.]

 4 Akupatseni zokhumba za mtima wanu,+

Ndipo akwaniritse zofuna zanu.+

 5 Tidzafuula mokondwera chifukwa cha chipulumutso chanu,+

Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.+

Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.+

 6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+

Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,+

Amamupulumutsa ndi dzanja lake lamanja lamphamvu zopulumutsa.+

 7 Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+

Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+

 8 Anthu amenewo athyoka ndipo agwa,+

Koma ife tanyamuka ndipo taima chilili.+

 9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+

Tsiku limene tidzaitana, Mulungu adzatiyankha.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikukondwera mu mphamvu zanu.+

Ndipo idzapitiriza kukondwera mu chipulumutso chanu.+

 2 Mwaipatsa zokhumba za mtima wake,+

Ndipo simunaimane zokhumba za pakamwa pake.+ [Seʹlah.]

 3 Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+

Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+

 4 Mfumuyo inakupemphani moyo. Ndipo munaipatsadi,+

Munaipatsa masiku ochuluka kuti ikhale mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

 5 Ulemerero wake ndi waukulu m’chipulumutso chanu.+

Mwaipatsa ulemu ndi ulemerero.+

 6 Mwaichititsa kukhala yodalitsika kwambiri mpaka muyaya.+

Mwaikondweretsa ndi kuisangalatsa pamaso panu.+

 7 Pakuti mfumu imakhulupirira Yehova,+

Imakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Wam’mwambamwamba. Iyo siidzagwedezeka.+

 8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse.+

Dzanja lanu lamanja lidzapeza odana nanu.

 9 Mudzawakhalitsa ngati oponyedwa mung’anjo yamoto pa nthawi ya kuonekera kwanu.+

Yehova adzawameza mu mkwiyo wake, ndipo moto udzawanyeketsa.+

10 Mudzawononga ana awo kuwachotsa padziko lapansi,+

Ndipo ana awo mudzawachotsa pakati pa ana a anthu.+

11 Pakuti akuchitirani zinthu zoipa.+

Alinganiza kuchita zinthu zimene sangazikwanitse.+

12 Inu mudzawachititsa kutembenuka ndi kuthawa.+

Mudzachita zimenezi ndi zingwe za mauta amene mwakonzekera kuwalasa nawo pankhope.+

13 Inu Yehova, mukhale wokwezeka mu mphamvu zanu.+

Tidzaimba ndi kutamanda mphamvu zanu.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe motsatira Mbawala Yaikazi ya M’bandakucha. Nyimbo ya Davide.

22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+

N’chifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?+

N’chifukwa chiyani simukumva mawu a kubuula kwanga?+

 2 Inu Mulungu wanga, ine ndimaitana usana koma simundiyankha.+

Usiku ndimaitanabe, moti sindikukhala chete.+

 3 Koma inu ndinu woyera.+

Mukukhala pakati pa zitamando za Isiraeli.+

 4 Makolo athu anali kudalira inu.+

Iwo anali kudalira inu ndipo munali kuwapulumutsa.+

 5 Iwo anali kufuulira inu,+ ndipo anali kupulumuka.+

Anali kudalira inu, ndipo simunawachititse manyazi.+

 6 Koma ine ndine nyongolotsi+ osati munthu.

Anthu amanditonza ndipo ndine wonyozeka kwa anthu.+

 7 Anthu onse ondiona amandinyodola.+

Iwo amandinyogodola ndi pakamwa pawo, ndipo amapukusa mitu yawo mondinyoza.+ Iwo amati:

 8 “Anadzipereka kwa Yehova.+ Amupulumutse Iyeyo!+

Ngati Mulungu amamukonda, amulanditse!”+

 9 Pakuti ndinu amene munanditulutsa m’mimba,+

Amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinali kuyamwa mabere a mayi anga.+

10 Ndinaponyedwa m’manja mwanu kuchokera m’mimba.+

Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.+

11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa zondisautsa zili pafupi,+

Ndiponso chifukwa ndilibe mthandizi winanso.+

12 Ng’ombe zazing’ono zamphongo zochuluka zandizungulira.+

Nkhunzi zamphamvu za ku Basana zandizinga.+

13 Iwo anditsegulira pakamwa pawo mondiopseza,+

Ngati mkango wokhadzula nyama umenenso ukubangula.+

14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.+

Mafupa anga onse alekanalekana.+

Mtima wanga wakhala ngati phula,+

Wasungunuka mkati mwanga.+

15 Mphamvu yanga yauma gwaa, ngati phale.+

Lilime langa lamamatira kunkhama zanga,+

Ndipo mwandikhazika m’fumbi la imfa.+

16 Agalu andizungulira.+

Khamu la anthu ochita zoipa landizinga.+

Iwo akuluma manja ndi mapazi anga ngati mkango.+

17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+

Adaniwo akuona zimenezi, ndipo akundiyang’anitsitsa.+

18 Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo,+

Ndipo akuchita maere pazovala zanga.+

19 Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine,+

Inu mphamvu yanga,+ ndithandizeni mofulumira.+

20 Landitsani moyo wanga ku lupanga,+

Moyo wanga wokhawu umene ndili nawo muulanditse m’kamwa mwa galu.+

21 Ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango,+

Ndipo mundiyankhe ndi kundipulumutsa ku nyanga za ng’ombe zamphongo zam’tchire.+

22 Ndidzalengeza dzina lanu+ kwa abale anga.+

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.+

23 Inu oopa Yehova, m’tamandeni!+

Inu nonse mbewu ya Yakobo, m’patseni ulemerero!+

Ndipo muopeni, inu nonse mbewu ya Isiraeli.+

24 Pakuti iye sananyoze,+

Kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa.+

Ndipo sanam’bisire nkhope yake.+

Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+

25 Chifukwa cha zimene mwachita ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+

Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu oopa iye.+

26 Ofatsa adzadya ndi kukhuta.+

Ofunafuna Yehova adzamutamanda.+

Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.+

27 Anthu onse okhala kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kubwerera kwa iye.+

Ndipo mafuko onse a anthu a mitundu ina adzagwada pamaso panu.+

28 Pakuti Yehova ndiye mfumu,+

Ndipo akulamulira mitundu.+

29 Anthu onse a padziko lapansi onyada chifukwa cha chuma chawo adzadya ndi kuwerama.+

Onse otsikira kufumbi adzawerama pamaso pake,+

Ndipo palibe amene adzapulumutsa moyo wake.+

30 Mbewu idzamutumikira.+

Adzalengeza za Yehova ku m’badwo wotsatira.+

31 Adzafika ndi kunena za chilungamo chake,+

Adzauza anthu amene adzabadwe kuti iye ndiye wachita zimenezi.+

Nyimbo ya Davide.

23 Yehova ndi M’busa wanga.+

Sindidzasowa kanthu.+

 2 Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri.+

Amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri.+

 3 Amatsitsimula moyo wanga.+

Amanditsogolera m’tinjira tachilungamo chifukwa cha dzina lake.+

 4 Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani,+

Sindikuopa kanthu,+

Pakuti inu muli ndi ine.+

Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.+

 5 Mumandipatsa chakudya patebulo, pamaso pa anthu ondichitira zoipa.+

Mwadzoza mutu wanga ndi mafuta.+

Chikho changa ndi chodzaza bwino.+

 6 Ndithudi, ubwino ndi kukoma mtima kosatha zidzanditsata masiku onse a moyo wanga.+

Ndipo ine ndidzakhala m’nyumba ya Yehova mpaka kalekale.+

Salimo la Davide.

24 Dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova,+

Nthaka ndi yake pamodzi ndi onse okhala panthakapo.+

 2 Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja,+

Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.+

 3 Ndani angakwere m’phiri la Yehova?+

Ndipo ndani anganyamuke kukalowa m’malo ake opatulika?+

 4 Aliyense wopanda mlandu m’manja mwake ndi woyera mumtima mwake,+

Amene sanaone Moyo wanga ngati wopanda pake,+

Kapena kulumbira mwachinyengo.+

 5 Ameneyo adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+

Adzalandira chilungamo kuchokera kwa Mulungu wa chipulumutso chake.+

 6 Umenewo ndiwo m’badwo wa amene amafunafuna Mulungu,

M’badwo wa anthu ofunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]

 7 “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+

Ndipo dzitukuleni, inu makomo akale lomwe,+

Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+

 8 “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”+

“Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+

Yehova wamphamvu mu nkhondo.”+

 9 “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+

Tukulani mitu, inu makomo akale lomwe,

Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+

10 “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”

“Ndi Yehova wa makamu. Iye ndiye Mfumu yaulemerero.”+ [Seʹlah.]

Salimo la Davide.

א [ʼAʹleph]

25 Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+

ב [Behth]

 2 Inu Mulungu wanga, chikhulupiriro changa chili mwa inu.+

Musalole kuti ndichite manyazi.

Adani anga asakondwere chifukwa cha masautso anga.+

ג [Giʹmel]

 3 Ndithudi, palibe aliyense amene adzachita manyazi mwa anthu amene chiyembekezo chawo chili mwa inu.+

Amene adzachite manyazi ndi amene akuchita zinthu mwachinyengo koma osaphula kanthu.+

ד [Daʹleth]

 4 Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+

Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu.+

ה [Heʼ]

 5 Ndiyendetseni m’choonadi chanu ndi kundiphunzitsa,+

Pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.+

ו [Waw]

Chiyembekezo changa chili mwa inu tsiku lonse.+

ז [Zaʹyin]

 6 Kumbukirani chifundo chanu,+ inu Yehova, ndi zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha.+

Pakuti munayamba kuchita zimenezo kale kwambiri.+

ח [Chehth]

 7 Musakumbukire machimo a pa unyamata wanga ndi zolakwa zanga.+

Ndikumbukireni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+

Ndiponso chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova.+

ט [Tehth]

 8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama.+

N’chifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende m’njira yoyenera.+

י [Yohdh]

 9 Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake,+

Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.+

כ [Kaph]

10 M’njira zonse za Yehova muli kukoma mtima kosatha ndi choonadi

Kwa anthu osunga pangano+ lake ndi zikumbutso zake.+

ל [Laʹmedh]

11 Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+

Mundikhululukire cholakwa changa ngakhale kuti n’chachikulu.+

מ [Mem]

12 Tsopano munthu woopa Yehova ndani?+

Adzamulangiza kuyenda m’njira imene adzasankha.+

נ [Nun]

13 Moyo wake udzasangalala ndi ubwino wa Mulungu,+

Mbadwa zake zidzatenga dziko lapansi kukhala lawo.+

ס [Saʹmekh]

14 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+

Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+

ע [ʽAʹyin]

15 Maso anga amayang’ana kwa Yehova nthawi zonse,+

Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+

פ [Peʼ]

16 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+

Pakuti ndasungulumwa ndipo ndasautsika.+

צ [Tsa·dheh]

17 Masautso a mtima wanga awonjezeka.+

Ndilanditseni ku nkhawa zimene zili pa ine.+

ר [Rehsh]

18 Onani masautso anga ndi mavuto anga,+

Ndipo mundichotsere machimo anga onse.+

19 Onani mmene adani anga achulukira,+

Ndipo chifukwa cha chidani chawo chachikulu, amafuna kundichitira chiwawa.+

ש [Shin]

20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa.+

Musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndathawira kwa inu.+

ת [Taw]

21 Mtima wanga wosagawanika ndiponso wowongoka unditeteze,+

Pakuti chiyembekezo changa chili mwa inu.+

22 Inu Mulungu, wombolani Isiraeli m’masautso ake onse.+

Salimo la Davide.

26 Ndiweruzeni,+ inu Yehova, pakuti ine ndayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika,+

Ndipo ndikudalira Yehova kuti ndisagwedezeke.+

 2 Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa.+

Yengani impso zanga ndi mtima wanga.+

 3 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha kuli pamaso panga.

Ine ndayenda m’choonadi chanu.+

 4 Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo.+

Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.+

 5 Ndimadana ndi mpingo wa anthu ochita zoipa,+

Ndipo sindikhala pansi ndi anthu oipa.+

 6 Ndidzasamba m’manja mwanga kusonyeza kuti ndine wopanda cholakwa,+

Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,+

 7 Kuti mawu anga oyamikira amveke kwambiri,+

Ndi kulengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+

 8 Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala+

Ndi malo amene kumakhala ulemerero wanu.+

 9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi anthu ochimwa,+

Kapena pamodzi ndi anthu a mlandu wamagazi.+

10 M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+

Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+

11 Koma ine ndidzayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+

Ndiwomboleni+ ndi kundikomera mtima.+

12 Phazi langa lidzaimadi pamalo athyathyathya.+

Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.+

Salimo la Davide.

27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+

Ndingaopenso ndani?+

Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+

Ndingachitenso mantha ndi ndani?+

 2 Anthu ochita zoipa atandiyandikira kuti adye mnofu wanga,+

Popeza kuti iwo ndi ondiukira komanso adani anga,+

Anapunthwa ndi kugwa.+

 3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,+

Mtima wanga sudzachita mantha.+

Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,+

Pameneponso ndidzadalira Mulungu.+

 4 Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova,+

Chimenecho ndi chimene ndimachikhumba,+

N’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+

Kuti ndione ubwino wa Yehova,+

Komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.+

 5 Pakuti pa tsiku la tsoka, iye adzandibisa m’malo ake otetezeka.+

Adzandibisa m’malo obisika m’hema wake.+

Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+

 6 Pamenepo mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani onse ondizungulira.+

Ndipo ndidzapereka nsembe za kufuula mokondwera pahema wake.+

Ndidzamuimbira nyimbo, ndithu ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.+

 7 Inu Yehova, imvani mawu anga pamene ndikuitana.+

Ndikomereni mtima ndi kundiyankha.+

 8 Mtima wanga wanena lamulo lanu lakuti: “Ndifunefuneni anthu inu.”+

Ndidzakufunafunani, inu Yehova.+

 9 Musandibisire nkhope yanu.+

Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.+

Inu mukhale mthandizi wanga.+

Musanditaye ndi kundisiya, inu Mulungu wa chipulumutso changa.+

10 Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+

Yehova adzanditenga.+

11 Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende m’njira yanu.+

Nditsogolereni m’njira yowongoka kuti nditetezeke kwa adani anga.

12 Musandipereke kwa adani anga.+

Pakuti mboni zonama zandiukira,+

Chimodzimodzinso munthu wachiwawa.+

13 Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.+

14 Yembekezera Yehova.+ Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+

Yembekezera Yehova.+

Salimo la Davide.

28 Ndikuitana inu Yehova.+

Inu Thanthwe langa, musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana,+

Kuti musakhale chete pamaso panga,+

Kutinso ine ndisafanane ndi amene akutsikira kudzenje la manda.+

 2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,

Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+

 3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+

Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+

 4 Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+

Mogwirizana ndi kuipa kwa zochita zawo.+

Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+

Abwezereni zochita zawo.+

 5 Pakuti iwo salabadira zochita za Yehova,+

Kapena ntchito za manja ake.+

Mulungu sadzawamanga koma adzawapasula.

 6 Adalitsike Yehova, chifukwa wamva kuchonderera kwanga.+

 7 Yehova ndiye mphamvu yanga+ ndi chishango changa.+

Mtima wanga umam’khulupirira.+

Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.+

Ndidzamutamanda mwa kumuimbira nyimbo yanga.+

 8 Yehova ndiye mphamvu kwa anthu ake,+

Iye ndi malo achitetezo odzetsa chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+

 9 Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+

Mukhale m’busa wawo ndipo muwanyamule mpaka kalekale.+

Salimo la Davide.

29 M’patseni Yehova, inu amphamvu,*

M’patseni Yehova ulemerero ndipo vomerezani kuti iye ndi wamphamvu.+

 2 M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+

Weramirani Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.+

 3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi,*+

Liwu la Mulungu waulemerero+ lagunda ngati bingu.+

Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+

 4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu,+

Liwu la Yehova ndi lokwezeka.+

 5 Liwu la Yehova likuthyola mitengo ya mkungudza,

Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+

 6 Iye akuichititsa kudumphadumpha ngati mwana wa ng’ombe,+

Lebanoni ndi Sirioni+ akudumphadumpha ngati ana a ng’ombe zakutchire.

 7 Liwu la Yehova likutulutsa malawi a moto.+

 8 Liwu la Yehova likuchititsa chipululu kuphiriphitha,+

Yehova akuchititsa chipululu cha Kadesi+ kuphiriphitha.

 9 Liwu la Yehova likuchititsa mbawala zazikazi kuphiriphitha ndi ululu wa pobereka,+

Ndipo likufafaniza nkhalango.+

M’kachisi wake aliyense akunena kuti: “Ulemerero ndi wa Mulungu!”+

10 Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa chigumula,*+

Ndipo Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+

11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+

Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.+

Nyimbo ndi Salimo la Davide lotsegulira nyumba.+

30 Ndidzakutamandani inu Yehova, pakuti mwandipulumutsa,+

Ndipo simunalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+

 2 Inu Yehova Mulungu wanga, ndinafuulira kwa inu kuti mundithandize ndipo munandichiritsa.+

 3 Inu Yehova, mwanditulutsa m’Manda,+

Mwandisunga ndi moyo, kuti ndisatsikire m’dzenje.+

 4 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, inu okhulupirika ake,+

Yamikani dzina lake loyera.*+

 5 Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+

Koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse.+

Usiku kumakhala kulira,+ koma m’mawa kumakhala kufuula ndi chisangalalo.+

 6 Mtima wanga utakhazikika ndinati:+

“Sindidzagwedezeka.”+

 7 Inu Yehova, chifukwa chakuti munandikomera mtima munakhazikitsa mwamphamvu phiri langa.+

Pamene munabisa nkhope yanu, ndinasokonezeka.+

 8 Ndinaitana inu Yehova,+

Ndipo ndinachonderera Yehova kuti andikomere mtima.+

 9 Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda?+

Kodi fumbi lidzakutamandani?+ Kodi lidzalengeza kuti inu ndinu woona?+

10 Imvani inu Yehova, ndi kundikomera mtima.+

Inu Yehova, khalani mthandizi wanga.+

11 Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.+

Mwandivula chiguduli* changa ndipo mwandiveka chisangalalo,+

12 Kuti mtima wanga uimbe nyimbo zokutamandani ndipo usakhale chete.+

Inu Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani mpaka kalekale.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

31 Ndathawira kwa inu Yehova.+

Musalole kuti ndichite manyazi.+

Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+

 2 Tcherani khutu lanu kwa ine.+

Ndilanditseni mofulumira.+

Mukhale thanthwe lolimba kwa ine,+

Mukhale nyumba ya mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+

 3 Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+

Chifukwa cha dzina lanu+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+

 4 Mudzandiwonjola mu ukonde umene anditchera,+

Pakuti inu ndinu malo anga achitetezo.+

 5 Ndikuikiza mzimu* wanga m’manja mwanu.+

Mwandiwombola,+ inu Yehova, Mulungu wachoonadi.+

 6 Ndimadana ndi olambira mafano opanda pake ndi achabechabe.+

Koma ine ndimadalira Yehova.+

 7 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha,+

Pakuti mwaona kusautsika kwanga.+

Mwadziwa zowawa zimene zandigwera,+

 8 Simunandipereke m’manja mwa adani.+

Mwapondetsa phazi langa pamalo otakasuka.+

 9 Ndikomereni mtima inu Yehova, pakuti ndasautsika kwambiri.+

Diso langa lafooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso moyo wanga ndi m’mimba mwanga.+

10 Chifukwa cha chisoni, moyo wanga watha,+

Ndipo chifukwa cha kuusa moyo kwanga, zaka zanga zafika kumapeto.+

Chifukwa cha zolakwa zanga, mphamvu zanga zafooka,+

Ndipo mafupa anga afooka.+

11 Ndakhala chitonzo+ pamaso pa onse odana nane,+

Ndipo kwa anthu oyandikana nawo ndakhala chitonzo chachikulu,+

Kwa anthu ondidziwa ndakhala woopsa.+

Akandiona ndili panja amandithawa.+

12 Ndaiwalidwa ngati munthu wakufa amene anthu sakumukumbukiranso.+

Ndakhala ngati chiwiya chosweka.+

13 Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+

Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+

Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+

Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+

14 Koma ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova.+

Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+

15 Moyo wanga uli m’manja mwanu.+

Ndilanditseni m’manja mwa adani anga ndi kwa anthu ondisakasaka.+

16 Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu.+

Ndipulumutseni mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

17 Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndaitana pa dzina lanu.+

Anthu oipa achite manyazi.+

Akhale chete m’Manda.+

18 Milomo yachinyengo isowe chonena,+

Milomo imene ikulankhula motsutsana ndi wolungama,+ yosadziletsa pa kudzikweza ndi kunyoza ena.+

19 Ubwino wanu,+ umene mwasungira anthu okuopani ndi wochuluka kwambiri!+

Ubwino umenewu mwapereka kwa anthu othawira kwa inu.

Mwaupereka kwa iwo, ana a anthu akuona.+

20 Mudzawabisa m’malo otetezeka pafupi ndi inu,+

Kuwachotsa pamaso pa anthu amene asonkhana pamodzi kuti awachitire chiwembu.+

Mudzawabisa mumsasa wanu kwa anthu ofuna kukangana nawo.+

21 Yehova adalitsike,+

Pakuti wandisonyeza modabwitsa kukoma mtima kosatha+ mumzinda wozingidwa ndi adani.+

22 Koma ine nditapanikizika ndinati:+

“Ndidzafafanizidwa kuchoka pamaso panu.”+

Ndithudi mwamva kuchonderera kwanga pamene ndinali kufuulira kwa inu kupempha thandizo.+

23 Kondani Yehova, inu nonse okhulupirika ake.+

Yehova amateteza okhulupirika,+

Koma aliyense wodzikuza adzamulanga mowirikiza.+

24 Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu,+

Inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.+

Salimo la Davide. Masikili.*

32 Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.+

 2 Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake,+

Amene alibe mtima wachinyengo.+

 3 Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga.+

 4 Pakuti dzanja lanu linali kundilemera usana ndi usiku.+

Mphamvu zanga zinauma ngati madzi m’nyengo yotentha ya chilimwe.+ [Seʹlah.]

 5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+

Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+

Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]

 6 Pa chifukwa chimenechi, aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu,+

Pa nthawi imene inu mungapezeke.+

Ndipo madzi ambiri osefukira sadzamukhudza ngakhale pang’ono.+

 7 Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+

Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.]

 8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+

Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+

 9 Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+

Imene munthu amachita kuimanga chingwe chapakamwa ndi chapamutu kuti athetse kupulupudza kwake,+

Ndi kuti aiyandikire.”+

10 Zopweteka za woipa ndi zambiri.

Koma wokhulupirira Yehova+ amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.+

11 Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.+

Fuulani ndi chisangalalo inu nonse owongoka mtima.+

33 Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova, inu nonse olungama.+

M’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.+

 2 Yamikani Yehova poimba zeze.+

Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.+

 3 Muimbireni nyimbo yatsopano.+

Muimbireni choimbira cha zingwe ndi mtima wonse ndi kufuula mosangalala.+

 4 Pakuti mawu a Yehova ndi owongoka,+

Ndipo ntchito zake zonse ndi zodalirika.+

 5 Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.+

Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.+

 6 Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+

Ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.+

 7 Anasonkhanitsa madzi a m’nyanja ngati wachita kuwatchinga ndi khoma,+

Anaika madzi amphamvu m’nyumba zosungiramo zinthu.

 8 Onse okhala padziko lapansi aope Yehova.+

Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.+

 9 Pakuti iye ananena, ndipo zinachitika.+

Iye analamula, ndipo zinakhalapo.+

10 Yehova wasokoneza zolinga za anthu a mitundu ina.+

Walepheretsa maganizo a mitundu ya anthu.+

11 Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+

Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

12 Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+

Anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.+

13 Kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana,+

Waona ana onse a anthu.+

14 Kuchokera kumalo achikhalire kumene iye amakhala,+

Wayang’anitsitsa onse okhala padziko lapansi.

15 Iye akuumba mtima wa aliyense wa iwo.+

Akulingalira ntchito zawo zonse.+

16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+

Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+

17 Hatchi siingabweretse chipulumutso,+

Siingapulumutse munthu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+

18 Taonani! Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa,+

Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha,+

19 Kuti apulumutse moyo wawo ku imfa,+

Ndi kuwasunga ndi moyo pa nthawi ya njala.+

20 Moyo wathu wakhala ukuyembekeza Yehova.+

Iye ndi mthandizi wathu ndi chishango chathu.+

21 Mitima yathu imakondwera mwa iye.+

Pakuti timadalira dzina lake loyera.+

22 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kukhale pa ife,+

Pakuti takhala tikuyembekezera inu.+

Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki* moti anam’pitikitsa ndipo Davideyo anathawa.

א [ʼAʹleph]

34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.+

Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.+

ב [Behth]

 2 Ndidzadzitamandira mwa Yehova.+

Ofatsa adzamva ndi kukondwera.+

ג [Giʹmel]

 3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine+ anthu inu,

Tiyeni tonse tikweze dzina lake.+

ד [Daʹleth]

 4 Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha,+

Pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.+

ה [Heʼ]

 5 Amene anamukhulupirira anasangalala,+

Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.+

ז [Zaʹyin]

 6 Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva.+

Anamupulumutsa m’masautso ake onse.+

ח [Chehth]

 7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu,+

Ndipo amawapulumutsa.+

ט [Tehth]

 8 Anthu inu, talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+

Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.+

י [Yohdh]

 9 Opani Yehova, inu oyera ake,+

Pakuti onse omuopa sasowa kanthu.+

כ [Kaph]

10 Mikango yamphamvu ingakhale ndi chakudya chochepa ndipo ingamve njala.+

Koma ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+

ל [Laʹmedh]

11 Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.+

Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+

מ [Mem]

12 Kodi munthu wokonda moyo ndani,+

Amene akufuna kukhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+

נ [Nun]

13 Tetezani lilime lanu ku zinthu zoipa,+

Ndi milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+

ס [Saʹmekh]

14 Patukani pa zinthu zoipa ndipo chitani zabwino.+

Funafunani mtendere ndi kuusunga.+

ע [ʽAʹyin]

15 Maso a Yehova ali pa olungama,+

Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+

פ [Peʼ]

16 Nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa,+

Kuti dzina lawo lisatchulidwenso padziko lapansi.+

צ [Tsa·dhehʹ]

17 Olungama anafuula, ndipo Yehova anamva,+

Iye anawapulumutsa m’masautso awo onse.+

ק [Qohph]

18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+

Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.+

ר [Rehsh]

19 Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka,+

Koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.+

ש [Shin]

20 Amateteza mafupa onse a wolungamayo.

Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+

ת [Taw]

21 Masoka adzapha munthu woipa.+

Ndipo wodana ndi munthu wolungama adzapezeka wolakwa.+

22 Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.+

Ndipo palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeka wolakwa.+

Salimo la Davide.

35 Weruzani mlandu wanga inu Yehova, motsutsana ndi adani anga.+

Menyani nkhondo ndi kugonjetsa amene akumenyana ndi ine.+

 2 Tengani chishango chaching’ono ndi chishango chachikulu,+

Ndipo bwerani kuti mundithandize.+

 3 Tengani mkondo ndi nkhwangwa ya pankhondo kuti mukumane ndi anthu amene akundilondalonda.+

Uzani moyo wanga kuti: “Ine ndine chipulumutso chako.”+

 4 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kunyozeka.+

Amene akundikonzera chiwembu muwabweze ndipo athedwe nzeru.+

 5 Akhale ngati mankhusu ouluzika ndi mphepo,+

Mngelo wa Yehova awapitikitse.+

 6 Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera,+

Ndipo mngelo wa Yehova aziwathamangitsa.

 7 Iwo andikumbira mbuna popanda chifukwa ndi kuikapo ukonde,+

Akumba mbunazo kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.+

 8 Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+

Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+

Agweremo ndi kuwonongeka.+

 9 Koma moyo wanga ukondwere mwa Yehova.+

Usangalale chifukwa cha chipulumutso chake.+

10 Ndinene ndi mtima wanga wonse kuti:+

“Inu Yehova, ndani angafanane ndi inu,+

Amene mumalanditsa wosautsika m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo,+

Amene mumalanditsa wozunzika ndi wosauka m’manja mwa munthu amene akumulanda zinthu zake?”+

11 Mboni zachiwawa zimaimirira.+

Zimandifunsa zinthu zimene sindikudziwa.+

12 Adani anga amandibwezera zoipa m’malo mwa zabwino,+

Ndipo ndimakhala wachisoni ngati wofedwa.+

13 Iwo akadwala ndinali kuvala chiguduli,+

Ndinali kusautsa moyo wanga mwa kusala kudya.+

Ndipo mapemphero anga anali kubwerera kwa ine osayankhidwa.+

14 Chifukwa cha mnzanga ndiponso m’bale wanga,+

Ndinamva chisoni kwambiri ngati munthu wolira maliro a mayi ake.+

Ndinawerama chifukwa cha chisoni.

15 Atandiona ndikuyenda motsimphina anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.+

Anasonkhana pamodzi kuti alimbane nane.+

Anandimenya pamene sindinali kuyembekezera.+

Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.+

16 Anthu ampatuko amene anali kunditonza kuti apeze kachakudya,+

Anandikukutira mano.+

17 Inu Yehova, kodi mudzayang’anira zimenezi kufikira liti?+

Ndipulumutseni kwa anthu ofuna kundiwononga,+

Pulumutsani moyo wanga+ ku mikango yamphamvu.

18 Ndidzakutamandani mu mpingo waukulu.+

Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.+

19 Musalole kuti anthu amene amadana ndi ine popanda chifukwa akondwere ndi kusautsika kwanga.+

Ndipo musalole kuti anthu amene amandida popanda chifukwa anditsinzinire diso.+

20 Iwo salankhula mawu amtendere,+

Koma amakonzera chiwembu anthu ofatsa a padziko lapansi,

Kuti awachitire zachinyengo.+

21 Amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane.+

Iwo amati: “Eya! Eya! Tadzionera tokha.”+

22 Inu Yehova, mwaona zimenezi+ ndipo musakhale chete.+

Musakhale patali ndi ine, inu Yehova.+

23 Nyamukani ndi kukhala maso kuti mundichitire chilungamo,+

Chitani zimenezi inu Mulungu wanga Yehova, kuti muweruze mlandu wanga.+

24 Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi chilungamo chanu,+

Musalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+

25 Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Izi ndi zimene timafuna.”+

Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+

26 Onse amene akukondwera ndi tsoka langa,+

Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+

Onse odzikweza pamaso panga achite manyazi+ ndi kutsitsidwa.+

27 Onse amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala ndi kukondwera.+

Nthawi zonse azinena kuti:+

“Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pa mtendere.”+

28 Lilime langa linene chapansipansi za chilungamo chanu,+

Ndipo likutamandeni tsiku lonse.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

36 Uchimo ukulankhula mumtima mwa munthu woipa.+

Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+

 2 Pakuti amadzinyenga yekha,+

Ndipo sazindikira cholakwa chake ndi kudana nacho.+

 3 Mawu a pakamwa pake ndi opweteka ndi achinyengo.+

Wasiya kugwiritsa ntchito nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.+

 4 Ali pabedi lake amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.+

Amaima panjira yoipa.+

Sapewa kuchita zinthu zoipa.+

 5 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba.+

Kukhulupirika kwanu kwafika m’mitambo.+

 6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+

Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+

Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+

 7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+

Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+

 8 Amadya ndi kukhuta chakudya chonona m’nyumba mwanu.+

Ndipo mumawamwetsa mumtsinje wa zosangalatsa zanu zambiri.+

 9 Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.+

Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.+

10 Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani,+

Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+

11 Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindipondereze.+

Ndipo musalole dzanja la anthu oipa kundipitikitsa kuti ndikhale wothawathawa.+

12 Onani, ochita zinthu zopweteka anzawo agwa.+

Awakanikizira pansi ndipo sakuthanso kudzuka.+

Salimo la Davide.

א [ʼAʹleph]

37 Usapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.+

Usakhumbe kukhala ngati anthu ochita zosalungama.+

 2 Pakuti adzafota mwamsanga ngati udzu,+

Adzanyala ngati msipu watsopano wobiriwira.+

ב [Behth]

 3 Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.+

Khala padziko lapansi, ndipo khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.+

 4 Komanso sangalala mwa Yehova,+

Ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.+

ג [Giʹmel]

 5 Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,+

Umudalire+ ndipo iye adzachitapo kanthu.+

 6 Iye adzaonetsa poyera kulungama kwako kuti kuunike ngati kuwala,+

Adzaonetsa poyera chilungamo chako kuti chiwale ngati usana.+

ד [Daʹleth]

 7 Khala chete pamaso pa Yehova,+

Ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse.+

Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendera bwino,+

Munthu amene akukwaniritsa zolinga zake zoipa.+

ה [Heʼ]

 8 Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.+

Usapse mtima kuti ungachite choipa.+

 9 Pakuti ochita zoipa adzaphedwa.+

Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi.+

ו [Waw]

10 Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+

Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+

11 Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+

Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+

ז [Zaʹyin]

12 Woipa akukonzera chiwembu munthu wolungama,+

Ndipo akumukukutira mano.+

13 Koma Yehova adzamuseka,+

Pakuti akuona kuti chimaliziro chake chifika.+

ח [Chehth]

14 Oipa asolola lupanga ndipo akunga uta wawo,+

Kuti agwetse osautsika ndi osauka,+

Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zowongoka.+

15 Lupanga lawo lidzalowa mumtima mwawo,+

Ndipo mauta awo adzathyoka.+

ט [Tehth]

16 Zinthu zochepa za munthu wolungama ndi zabwino+

Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+

17 Pakuti manja a anthu oipa adzathyoledwa,+

Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.+

י [Yohdh]

18 Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa,+

Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+

19 Pa nthawi yatsoka sadzachita manyazi,+

Ndipo pa nthawi ya njala adzakhuta.+

כ [Kaph]

20 Pakuti anthu oipa adzatheratu onse,+

Ndipo adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso.

Iwo adzatha.+ Adzazimiririka ndi kusanduka utsi.+

ל [Laʹmedh]

21 Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza,+

Koma wolungama amakomera mtima ena ndipo amapereka mphatso.+

22 Anthu amene Mulungu akuwadalitsa adzalandira dziko lapansi,+

Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+

מ [Mem]

23 Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake,+

Ndipo Mulungu amakondwera ndi njira zake.+

24 Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+

Pakuti Yehova wamugwira dzanja.+

נ [Nun]

25 Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula,+

Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+

Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+

26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+

Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+

ס [Saʹmekh]

27 Patuka pa choipa ndipo uchite chabwino,+

Ukatero udzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.+

28 Pakuti Yehova amakonda chilungamo,+

Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+

ע [ʽAʹyin]

Adzawateteza mpaka kalekale.+

Koma ana a anthu oipa adzaphedwa.+

29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+

Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.+

פ [Peʼ]

30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,+

Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+

31 Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+

Poyenda mapazi ake sadzaterereka.+

צ [Tsa·dhehʹ]

32 Woipa amalondalonda munthu wolungama,+

Ndipo amafuna kuti amuphe.+

33 Koma Yehova sadzasiya wolungama m’manja mwa woipayo,+

Ndipo pamene wolungamayo akuweruzidwa, Mulungu sadzamuona monga wolakwa.+

ק [Qohph]

34 Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake,+

Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.+

Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.+

ר [Rehsh]

35 Ine ndaona munthu woipa, wolamulira mwankhanza+

Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo waukulu wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+

36 Koma anafa ndipo sanapezekenso.+

Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+

ש [Shin]

37 Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama,+

Pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere.+

38 Koma anthu onse ochimwa adzafafanizidwa.+

M’tsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+

ת [Taw]

39 Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+

Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya nsautso.+

40 Yehova adzawathandiza ndi kuwapulumutsa.+

Adzawapulumutsa kwa anthu oipa ndi kuwalanditsa,+

Chifukwa athawira kwa iye.+

Nyimbo ya Davide ya chikumbutso.

38 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,+

Kapena kundilanga mutapsa mtima.+

 2 Pakuti mivi yanu yandilasa kwambiri,+

Ndipo dzanja lanu likundilemera.+

 3 Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+

Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+

 4 Pakuti zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+

Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.+

 5 Zilonda zanga zanunkha ndi kunyeka,

Chifukwa cha kupusa kwanga.+

 6 Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+

Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+

 7 M’chiuno mwanga mukutentha kwambiri,

Ndipo palibe paliponse pabwino m’thupi langa.+

 8 Ndalefuka ndipo ndaponderezeka kwambiri.

Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.+

 9 Inu Yehova, zokhumba zanga zonse zili pamaso panu,

Kudandaula kwanga sikunabisike kwa inu.+

10 Mtima wanga ukugunda kwambiri, ndipo mphamvu zanga zatha,

Maso anga achita mdima.+

11 Anthu amene anali kundikonda ndiponso anzanga aima patali chifukwa cha kuvutika kwanga,+

Ndipo mabwenzi anga apamtima anditalikira.+

12 Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+

Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+

Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+

13 Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha, sindikumvetsera,+

Ndakhala ngati munthu wosalankhula, sindikutsegula pakamwa.+

14 Ndakhala ngati munthu wosamva,

Sindikulankhula zotsutsana nawo.

15 Pakuti ine ndikuyembekezera inu Yehova.+

Inu Yehova Mulungu wanga, mudzandiyankha.+

16 Ine ndinati: “Ngati simundiyankha adani anga adzasangalala chifukwa cha kusautsika kwanga.+

Phazi langa likaterereka,+ iwo adzadzikweza pamaso panga.”+

17 Ndinali pafupi kupunthwa,+

Ndipo ndinali kumva ululu nthawi zonse.+

18 Pakuti ndinali kulankhula za cholakwa changa.+

Ndipo ndinali kudera nkhawa za tchimo langa.+

19 Adani anga anali amphamvu kwambiri,+

Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.+

20 Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+

Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+

21 Inu Yehova, musandisiye.

Inu Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.+

22 Fulumirani kundithandiza,+

Inu Yehova, chipulumutso changa.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide.

39 Ine ndinati: “Ndidzatchinjiriza njira zanga,+

Kuti ndisachimwe ndi lilime langa.+

Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke,+

Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”+

 2 Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+

Ndinakhala phee osanena ngakhale zinthu zabwino,+

Ndipo ndinanyalanyaza ululu wanga.

 3 Mumtima mwanga munatentha moto.+

Pamene ndinali kuusa moyo, moto unali kuyakabe.

Choncho ndinati:

 4 “Inu Yehova, ndidziwitseni za kufulumira kwa chimaliziro changa,+

Ndiponso kuti masiku anga ndi ochepa motani,+

Kuti ndidziwe kufupika kwa moyo wanga.+

 5 Taonani! Mwachepetsa masiku anga.+

Ndipo nthawi ya moyo wanga si kanthu pamaso panu.+

Ndithudi, munthu aliyense ngakhale atakhala wamphamvu bwanji, sali kanthu koma ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ [Seʹlah.]

 6 Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+

Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+

Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+

 7 Nanga tsopano, inu Yehova, ine ndikuyembekezera chiyani?

Chiyembekezo changa chili mwa inu.+

 8 Ndilanditseni ku zolakwa zanga zonse.+

Musalole kuti munthu wopusa azinditonza.+

 9 Ndinakhala chete.+ Sindinatsegule pakamwa panga,+

Pakuti inu munachitapo kanthu.+

10 Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera.+

Ine ndatha chifukwa cha ukali wa dzanja lanu.+

11 Mwa kudzudzula cholakwa, mwawongolera munthu,+

Ndipo mwawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete*+ imachitira.

Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ [Seʹlah.]

12 Imvani pemphero langa, inu Yehova,

Ndipo tcherani khutu pamene ndikufuula kupempha thandizo.+

Musandinyalanyaze pamene ndikugwetsa misozi.+

Pakuti ndine mlendo wanu,+

Mlendo wokhala nanu monga anachitira makolo anga onse.+

13 Musandiyang’ane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalala+

Ndisanamwalire ndi kuiwalika.”+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

40 Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,+

Choncho iye anatchera khutu kwa ine ndipo anamva kufuula kwanga kopempha thandizo.+

 2 Iye ananditulutsanso m’dzenje la madzi a mkokomo,+

Ananditulutsa m’chithaphwi cha matope.+

Kenako anapondetsa phazi langa pathanthwe.+

Anandiyendetsa panthaka yolimba.+

 3 Komanso anaika mawu a nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,

Nyimbo yotamanda Mulungu wathu.+

Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,+

Iwo adzakhulupirira Yehova.+

 4 Wodala ndi munthu wamphamvu amene amakhulupirira Yehova,+

Munthu amene sanacheukire anthu otsutsa,

Kapena anthu amene anapatukira m’njira za mabodza.+

 5 Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa,+

Ndipo mumatiganizira.+

Palibe angafanane ndi inu.+

Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo,

Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

 6 Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo.+

Inu munatsegula makutu anga.+

Simunapemphe nsembe yopsereza ndi nsembe yamachimo.+

 7 Chifukwa cha zimenezo ndinati: “Ine ndabwera,+

Pakuti mumpukutu munalembedwa za ine.+

 8 Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga,+

Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+

 9 Ndanena za uthenga wabwino wachilungamo mumpingo waukulu.+

Onani! Sindinatseke pakamwa panga.+

Inu Yehova, mukudziwa bwino zimenezi.+

10 Chilungamo chanu sindinachibise mumtima mwanga.+

Ndinalengeza za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.+

Sindinabise kukoma mtima kwanu kosatha ndi choonadi chanu mumpingo waukulu.”+

11 Inu Yehova, musasiye kundimvera chisoni.+

Kukoma mtima kwanu kosatha komanso choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.+

12 Pakuti masoka anandizungulira moti sindinathe kuwawerenga.+

Zolakwa zanga zochuluka zinandifikira modzidzimutsa moti sindinathe kuziona mmene zinachulukira.+

Zinachuluka kwambiri kuposa tsitsi la kumutu kwanga,+

Ndipo ndinataya mtima.+

13 Khalani wofunitsitsa kundilanditsa, inu Yehova.+

Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+

14 Onse amene akufunafuna moyo wanga kuti aufafanize+

Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+

Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+

15 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”+

Ayang’anitsitse modabwa chifukwa cha manyazi awo.+

16 Onse amene akufunafuna inu,+

Akondwere ndi kusangalala mwa inu.+

Onse amene amakonda chipulumutso chanu,+

Nthawi zonse azinena kuti: “Yehova alemekezeke.”+

17 Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+

Yehova amandiwerengera.+

Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+

Inu Mulungu wanga musachedwe.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+

Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+

 2 Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.+

Adzatchedwa wodala padziko lapansi.+

Ndipo Mulungu sangamupereke kwa adani ake.+

 3 Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+

Mudzamusamalira bwino kwambiri pamene akudwala.+

 4 Koma ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+

Ndichiritseni, pakuti ndakuchimwirani.”+

 5 Adani anga amanena zoipa zokhazokha za ine kuti:+

“Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake lifafanizike?”

 6 Wina akabwera kudzandiona, amalankhula zabodza kuchokera mumtima mwake.+

Amasonkhanitsa nkhani zoipa.

Akatero amachoka, ndipo kunjako amauza ena zabodza zokhudza ine.+

 7 Mogwirizana, onse amene amadana nane amanong’onezana kuti andiukire.+

Amandikonzera chiwembu kuti andichitire zinthu zoipa. Iwo amati:+

 8 “Amutsanulira tsoka.*+

Tsopano popeza iye wagona, sadzukanso.”+

 9 Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+

Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+

10 Koma inu Yehova, ndikomereni mtima ndi kundidzutsa,+

Kuti ndiwabwezere.+

11 Mukatero ndidziwa kuti mwasangalala nane,

Chifukwa mdani wanga sadzafuula mosangalala kuti wandipambana.+

12 Koma ine mwandichirikiza chifukwa cha mtima wanga wosagawanika,+

Ndipo mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.+

13 Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+

Kuyambira kalekale mpaka kalekale.+

Ame! Ame!*+

BUKU LACHIWIRI

(Masalimo 42 – 72)

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili* ya ana a Kora.+

42 Monga mmene mbawala yaikazi imalakalakira mitsinje ya madzi,

Moyo wanganso ukulakalaka inu Mulungu wanga.+

 2 Moyo wanga ukulakalaka Mulungu,+ ukulakalaka Mulungu wamoyo.+

Ndidzapita liti kunyumba ya Mulungu kukaonekera pamaso pake?+

 3 Misozi yanga yasanduka chakudya changa usana ndi usiku,+

Pamene anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+

 4 Ndidzakumbukira zinthu zakale ndipo moyo wanga udzavutika pokumbukira zimenezo.+

Pakuti ndinali kuyenda ndi khwimbi la anthu,

Ndinali kuyenda pang’onopang’ono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,+

Tinali kufuula mosangalala ndi kuyamika Mulungu.+

Khamu la anthu okondwerera madyerero linali kunditsatira.+

 5 N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+

Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+

Yembekezera Mulungu,+

Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu.+

 6 Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima.+

N’chifukwa chake ndakumbukira inu,+

Pamene ndili m’dziko la Yorodano ndi m’mapiri a Herimoni,+

Pamene ndili m’phiri laling’ono.+

 7 Madzi akuya akufuulira madzi akuya,

Kudzera mu mkokomo wa madzi otumphuka.

Mafunde anu onse amphamvu,+

Andimiza.+

 8 Masana Yehova adzalamula kukoma mtima kwake kosatha kuti kufike pa ine,+

Ndipo usiku ndidzaimba za iye.+

Ndidzapemphera kwa Mulungu wondipatsa moyo.+

 9 Ndidzauza Mulungu, thanthwe langa kuti:+

“N’chifukwa chiyani mwandiiwala?+

Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?”+

10 Odana nane akunditonza kwambiri moti zikungokhala ngati mafupa anga aphwanyidwa,+

Pakuti anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+

11 N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+

Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+

Yembekezera Mulungu,+

Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndiponso ndiye Mulungu wanga.+

43 Ndiweruzeni+ inu Mulungu,

Weruzani mlandu wanga+ motsutsana ndi mtundu wosakhulupirika.

Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo ndi wochita zosalungama.+

 2 Pakuti inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+

N’chifukwa chiyani mwanditaya?

Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?+

 3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+

Zimenezi zinditsogolere.+

Zindifikitse kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+

 4 Ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+

Kwa Mulungu amene amandikondweretsa ndi kundisangalatsa.+

Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze, inu Mulungu, Mulungu wanga.+

 5 N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+

Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?

Yembekezera Mulungu,+

Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndi Mulungu wanga.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Masikili.*

44 Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,

Makolo athu anatifotokozera+

Ntchito zimene inu munachita m’masiku awo,+

M’masiku akale.+

 2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+

Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+

Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+

 3 Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,+

Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.+

Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,

Chifukwa munakondwera nawo.+

 4 Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga.+

Lamulani kuti Yakobo alandire chipulumutso chachikulu.+

 5 Ndi thandizo lanu tidzakankha adani athu.+

M’dzina lanu tidzapondereza amene akutiukira.+

 6 Pakuti sindinadalire uta wanga,+

Ndipo si lupanga langa limene linandipulumutsa.+

 7 Ndinu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+

Ndipo munanyazitsa anthu amene amadana nafe kwambiri.+

 8 Tidzayamika Mulungu nthawi zonse,+

Tidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]

 9 Koma tsopano mwatitaya ndi kutichititsa manyazi,+

Simukuyenda ndi magulu athu ankhondo.+

10 Mwachititsa kuti tithawe pamaso pa adani athu,+

Ndipo anthu odana nafe kwambiri afunkha zinthu zathu.+

11 Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,+

Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+

12 Mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika kwambiri,+

Ndipo simunapeze phindu ndi mtengo wawo.

13 Mwatisandutsa chitonzo kwa anthu oyandikana nafe,+

Mwatisandutsa chinthu chonyozeka ndi choseketsa kwa onse otizungulira.+

14 Mwatisandutsa mwambi pakati pa anthu a mitundu ina,+

Mwatisandutsa anthu amene anthu a mitundu inawo akuwapukusira mitu.+

15 Zondichititsa manyazi zili pamaso panga tsiku lonse,

Ndipo manyazi aphimba nkhope yanga,+

16 Chifukwa cha mawu a munthu wonditonza ndi wolankhula zachipongwe,

Ndiponso chifukwa cha mdani wanga ndi wofuna kundibwezera choipa.+

17 Zonsezi ndi zimene zatigwera, koma sitinakuiwaleni,+

Sitinachite mwachinyengo ndi pangano lanu.+

18 Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika n’kuchoka panjira yanu,+

Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu.+

19 Pakuti inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imasonkhana,+

Mwatiphimba ndi mdima wandiweyani.+

20 Ngati tikanaiwala dzina la Mulungu wathu,

Kapena kupemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu,+

21 Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+

Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+

22 Koma chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse.

Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.+

23 Nyamukani. N’chifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+

Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+

24 N’chifukwa chiyani mukubisabe nkhope yanu?

N’chifukwa chiyani mukuiwala masautso athu ndi kuponderezedwa kwathu?+

25 Pakuti miyoyo yathu yasautsika.+

Mimba zathu zili thasa! padothi.

26 Nyamukani kuti mutithandize+

Tiwomboleni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.* Salimo la ana a Kora. Masikili.* Nyimbo yonena za akazi okondedwa.

45 Mtima wanga wagalamuka chifukwa cha nkhani yosangalatsa.+

Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za mfumu.”+

Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera malemba waluso.+

 2 Ndiwedi wokongola kwambiri kuposa ana a anthu.+

Mawu otuluka m’kamwa mwako ndi osangalatsadi.+

N’chifukwa chake Mulungu adzakupatsa madalitso mpaka kalekale.+

 3 Mangirira lupanga lako+ m’chiuno mwako wamphamvu iwe,+

Limodzi ndi ulemu ndiponso ulemerero wako.+

 4 Ndipo upambane mu ulemerero wako.+

Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+

Ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.+

 5 Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu,+

Mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ako.+

 6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+

 7 Umakonda chilungamo+ ndipo umadana ndi zoipa.+

N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako,+ wakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu+ kuposa cha mafumu ena.+

 8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+

Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+

 9 Ana aakazi+ a mafumu ali m’gulu la akazi ako okondedwa.

Mkazi wamkulu wa mfumu+ waima kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+

10 Iwe mwana wanga wamkazi, mvetsera ndipo ona ndi kutchera khutu.

Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.+

11 Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,+

Pakuti ndiyo mbuye wako,+

Choncho iweramire.+

12 Mwana wamkazi wa ku Turo alinso komweko ndi mphatso,+

Olemera pakati pa anthu adzakhazika pansi mtima wako.+

13 Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu m’nyumba ya mfumu.+

Zovala zake ndi zagolide.

14 Adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.+

Anamwali anzake omuperekeza akubwera nawo kwa iwe.+

15 Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.

Ndipo adzalowa m’nyumba ya mfumu.

16 Ana anu adzatenga+ malo a makolo anu,+

Ndipo mudzawaika kukhala akalonga padziko lonse lapansi.+

17 Ndidzatchula dzina lanu m’mibadwo yonse yam’tsogolo.+

N’chifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora+ mogwirizana ndi kaimbidwe ka Atsikana.

46 Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu,+

Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.+

 2 N’chifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,+

Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka ndi kumira m’nyanja yaikulu.+

 3 Ngakhale madzi a m’nyanjayo atawinduka ndi kuchita thovu,+

Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha phokoso la nyanja yaikuluyo.+ [Seʹlah.]

 4 Pali mtsinje womwe nthambi zake zimachititsa anthu a mumzinda wa Mulungu kukondwera,+

Chihema chachikulu chopatulika koposa cha Wam’mwambamwamba.+

 5 Mulungu ali pakati pa mzinda.+ Mzindawo sudzagwedezeka.+

Mulungu adzauthandiza m’bandakucha.+

 6 Mitundu ya anthu inachita phokoso,+ maufumu anagwedezeka.

Iye anatulutsa mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+

 7 Yehova wa makamu ali ndi ife.+

Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]

 8 Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova,+

Onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.+

 9 Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.+

Ndipo watentha magaleta pamoto.+

10 “Gonjerani anthu inu, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu.+

Ndidzakwezedwa pakati pa anthu a mitundu ina,+

Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+

11 Yehova wa makamu ali ndi ife.+

Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.

47 Ombani m’manja anthu nonsenu.+

Fuulirani Mulungu mokondwera chifukwa chakuti wapambana.+

 2 Pakuti Yehova, Wam’mwambamwamba, ndi wochititsa mantha,+

Ndiye Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+

 3 Iye adzagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika pansi pathu.+

Adzagonjetsa anthu a mitundu ina ndi kuwaika pansi pa mapazi athu.+

 4 Adzatisankhira cholowa,+

Chimene Yakobo, amene amamukonda, anakondwera nacho.+ [Seʹlah.]

 5 Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mokondwera,+

Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+

 6 Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.+

Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.

 7 Pakuti Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+

Imbani nyimbo zotamanda ndi kuchita zinthu mozindikira.+

 8 Mulungu wakhala mfumu ya mitundu ya anthu.+

Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.+

 9 Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana.+

Asonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.+

Pakuti anthu onse omwe ali ngati zishango* za dziko lapansi ndi a Mulungu.+

Iye wakwera pamalo okwezeka kwambiri.+

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

48 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+

Mumzinda wa Mulungu wathu,+ m’phiri lake loyera.+

 2 Phiri la Ziyoni limene lili m’dera lakutali la kumpoto,+

Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka ndi osangalatsa padziko lonse lapansi,+

Mudzi wa Mfumu Yaikulu.+

 3 Munsanja zokhalamo za m’mudzimo, Mulungu wadziwika kuti ndi malo okwezeka ndiponso achitetezo.+

 4 Taonani! Mafumu anakumana atapangana,+

Koma anangodutsa.+

 5 Iwo anaona ndipo anadabwa.

Anasokonezeka, moti anathawa mopanikizika kwambiri.+

 6 Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,+

Anamva zopweteka ngati za mkazi amene akubereka.+

 7 Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kum’mawa, munaswa zombo za ku Tarisi.+

 8 Ife taona zimene Mulungu anachita monga mmene tinamvera,+

Mumzinda wa Yehova wa makamu, mumzinda wa Mulungu wathu.+

Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]

 9 Inu Mulungu, ife talingalira mozama za kukoma mtima kwanu kosatha,+

Tili mkati mwa kachisi wanu.+

10 Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu,+ kukutamandani

Kwafika kumalire a dziko lapansi.

Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+

11 Phiri la Ziyoni+ likondwere,

Midzi yozungulira Yuda isangalale+ chifukwa cha zigamulo zanu.+

12 Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo,+

Werengani nsanja zake.+

13 Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba.+

Yenderani nsanja zake zokhalamo,

Kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.+

14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

Iye adzatitsogolera kufikira imfa yathu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

49 Mvetserani izi, anthu nonsenu.

Tcherani khutu inu nonse a m’nthawi* ino,+

 2 Inu mtundu wa anthu ndiponso inu ana a anthu,

Inu olemera pamodzi ndi inu osauka.+

 3 Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,+

Ndipo zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zinthu zakuya.+

 4 Ndidzatchera khutu kuti ndimvetsere mwambi.+

Poimba zeze ndidzamasulira mawu anga ophiphiritsa.+

 5 Ndichitirenji mantha m’masiku oipa,+

Pamene zolakwa za ofuna kundigwetsa zandizinga?+

 6 Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+

Amene akudzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+

 7 Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake,+

Kapena kumuperekera dipo* kwa Mulungu,

 8 (Ndipo malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali,+

Moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale)

 9 Kuti akhale ndi moyo mpaka muyaya osaona dzenje la manda.+

10 Pakuti amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,+

Wopusa ndi wopanda nzeru, onsewo amawonongeka,+

Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+

11 Zokhumba za mtima wawo n’zakuti nyumba zawo zikhalebe mpaka kalekale,+

Mahema awo akhalebe ku mibadwomibadwo.+

Malo awo amawatcha mayina awo.+

12 Komabe munthu wochokera kufumbi, ngakhale atakhala wolemekezeka, sangakhale ndi moyo mpaka kalekale.+

Iye amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+

13 Umu ndi mmene zimakhalira ndi zitsiru,+

Komanso amene amazitsanzira, omwe amasangalala ndi mawu awo odzitukumula. [Seʹlah.]

14 Awatsogolera ku Manda ngati nkhosa zopita kokaphedwa.+

Imfa idzakhala m’busa wawo.+

Ndipo m’mawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+

Matupi awo adzawonongeka.+

Aliyense wa iwo malo ake okhala ndi ku Manda, osati malo okwezeka.+

15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga ku Manda,+

Pakuti adzandilandira. [Seʹlah.]

16 Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina akupeza chuma,+

Kapena chifukwa chakuti ulemerero wa nyumba yake ukuwonjezeka,+

17 Pakuti pa imfa yake sangatenge kena kalikonse.+

Ulemerero wake sudzapita naye pamodzi.+

18 Pakuti pamene anali moyo anali kutamanda moyo wake,+

(Ndipo anthu adzakutamanda chifukwa chakuti walemera)+

19 Moyo wake udzafanana ndi wa m’badwo wa makolo ake.+

Ndipo iwo sadzaonanso kuwala.+

20 Munthu, ngakhale atakhala wolemekezeka, koma ngati ali wosazindikira,+

Amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+

Nyimbo ya Asafu.+

50 Wamphamvuyo,+ Yehova, Mulungu,+ walankhula+

Ndipo akuitana dziko lapansi,+

Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.+

 2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni,+ mzinda wokongola kwambiri.+

 3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+

Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+

Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+

 4 Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+

Kuti apereke chiweruzo kwa anthu ake. Iye akuti:+

 5 “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,+

Amene achita pangano mwa kupereka nsembe.”+

 6 Ndipo kumwamba kukunena za chilungamo chake,+

Pakuti Mulungu ndiye Woweruza.+ [Seʹlah.]

 7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,+

Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+

Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+

 8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,+

Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+

 9 Sindidzatenga ng’ombe yamphongo m’nyumba yanu,+

Kapena mbuzi yamphongo m’makola anu.

10 Pakuti nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+

Ndiponso nyama zopezeka m’mapiri 1,000.+

11 Ndikudziwa bwino zolengedwa zonse zouluka za m’mapiri,+

Ndipo magulu a nyama zakutchire ndi anga.+

12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuze,

Pakuti dziko lonse+ ndiponso zonse za mmenemo ndi zanga.+

13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ng’ombe zamphongo zonenepa,+

Kapena kumwa magazi a mbuzi zamphongo?+

14 Pereka nsembe zoyamikira kwa Mulungu,+

Ndipo pereka kwa Wam’mwambamwamba zimene walonjeza.+

15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+

Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+

16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:+

“Ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+

Ndi wolankhula za pangano langa?+

17 Iwe umadana ndi malangizo,*+

Ndipo umaponya mawu anga kunkhongo.+

18 Nthawi zonse ukaona wakuba unali kusangalala naye.+

Ndipo unali kugwirizana ndi anthu achigololo.+

19 Walekerera pakamwa pako kulankhula zinthu zoipa,+

Ndipo ukugwiritsa ntchito lilime lako kulankhula zachinyengo.+

20 Umakhala pansi ndi kunenera m’bale wako zinthu zoipa,+

Umapezera zifukwa mwana wamwamuna wa mayi ako.+

21 Wachita zinthu zonsezi, koma ine ndinakhala chete.+

Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.+

Ine ndidzakudzudzula,+ ndipo ndidzaika machimo ako onse poyera iwe ukuona.+

22 Zindikirani zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+

Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.+

23 Amene akupereka nsembe yoyamikira kwa ine ndi amene akundilemekeza.+

Ndipo amene akuyenda panjirayo motsimikiza,

Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. Pa nthawi imene mneneri Natani anapita kwa Davide atagona ndi Bati-seba.+

51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+

Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+

 2 Mundisambitse bwinobwino ndi kuchotsa cholakwa changa,+

Ndiyeretseni ku tchimo langa.+

 3 Pakuti zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino,+

Ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.+

 4 Ine ndakuchimwirani kwambiri,+

Ndipo ndachita chinthu choipa pamaso panu,+

Choncho mukamalankhula mumalankhula zachilungamo,+

Ndipo mukamaweruza, mumaweruza molungama.+

 5 Taonani! Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa.+

Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+

 6 Taonani! Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.+

Ndipo mundidziwitse nzeru mumtima mwanga.+

 7 Ndiyeretseni ndi hisope ku machimo anga kuti ndikhale woyera.+

Ndisambitseni kuti ndiyere kwambiri kuposa chipale chofewa.+

 8 Ndichititseni kumva kufuula kokondwera ndi kosangalala,+

Kuti munthu* amene mwamuthyola akondwere.+

 9 Ndikhululukireni machimo anga,+

Ndipo fafanizani zolakwa zanga zonse.+

10 Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga,+

Ndipo ikani maganizo* atsopano ndi okhazikika mwa ine.+

11 Musandichotse pamaso panu ndi kunditaya.+

Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera.+

12 Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chifukwa cha chipulumutso chanu,+

Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.+

13 Anthu ophwanya malamulo ndidzawaphunzitsa njira zanu,+

Kuti ochimwa abwerere kwa inu.+

14 Inu Mulungu, ndilanditseni ku mlandu wa magazi,+ inu Mulungu wa chipulumutso changa,+

Kuti lilime langa linene za chilungamo chanu mokondwera.+

15 Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi,+

Kuti pakamwa panga patamande inu.+

16 Pakuti nsembe singakusangalatseni, chifukwa ikanakusangalatsani ndikanaipereka kwa inu.+

Nsembe yopsereza yathunthu singakusangalatseni.+

17 Kudzimvera chisoni mumtima ndizo nsembe zimene Mulungu amavomereza.+

Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.+

18 Chitirani Ziyoni zabwino mwa kukoma mtima kwanu.+

Ndipo mangani mpanda wa Yerusalemu.+

19 Mukatero mudzakondwera ndi nsembe zachilungamo,+

Mudzakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zathunthu.+

Pamenepo ng’ombe zamphongo zidzaperekedwa paguwa lanu la nsembe.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi, Mwedomu, anapita kwa Sauli kukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+

52 N’chifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa, wamphamvu iwe?+

Kukoma mtima kosatha kwa Mulungu n’kokhalitsa.+

 2 Lilime lako limakonza chiwembu, ndipo ndi lakuthwa ngati lezala,+

Limachita zachinyengo.+

 3 Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,+

Umakonda kwambiri kulankhula chinyengo kuposa kulankhula chilungamo.+ [Seʹlah.]

 4 Umakonda mawu onse owononga,+

Lilime lachinyengo iwe.+

 5 Mulungu adzakupasula kosatha.+

Adzakugwetsa ndi kukukokera kunja kwa hema wako,+

Ndipo adzakuzula ndithu m’dziko la anthu amoyo.+ [Seʹlah.]

 6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha,+

Ndipo adzamuseka.+

 7 Munthu wamphamvu wotere sadalira Mulungu monga malo ake achitetezo,+

Koma amadalira kuchuluka kwa chuma chake,+

Ndipo chitetezo chake amachipeza m’mavuto amene iyeyo amawachititsa.+

 8 Koma ine ndidzakhala ngati mtengo waukulu wa maolivi+ wa masamba obiriwira m’nyumba ya Mulungu.

Ndidzakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Mulungu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

 9 Ndidzakutamandani mpaka kalekale, chifukwa cha zimene mwachita.+

Ndipo ndidzayembekezera dzina lanu pamaso pa okhulupirika anu, chifukwa ndi labwino.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.*+ Masikili.* Salimo la Davide.

53 Wopusa amanena mumtima mwake kuti:

“Kulibe Yehova.”+

Anthu oterewa amachita zoipa, ndipo amachita zinthu zonyansa zogwirizana ndi kupanda chilungamo kwawo.+

Palibe amene akuchita zabwino.+

 2 Koma kuchokera kumwamba, Mulungu wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+

Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+

 3 Onse abwerera, ndipo onsewo ndi achinyengo.+

Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+

Palibiretu ndi mmodzi yemwe.

 4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+

Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+

Iwo sanaitane pa Yehova.+

 5 Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+

Ngakhale kuti panalibe chochititsa mantha.+

Pakuti Mulungu adzamwaza mafupa a aliyense womanga msasa kuti akuukireni.+

Isiraeli adzawachititsa manyazi pakuti Yehova wawakana.+

 6 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+

Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+

Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kwathu?”+

54 Inu Mulungu, ndipulumutseni m’dzina lanu,+

Ndipo ndithandizeni ndi mphamvu zanu.+

 2 Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+

Tcherani khutu ku mawu ochokera m’kamwa mwanga.+

 3 Pakuti pali anthu achilendo amene andiukira,

Ndipo pali olamulira ankhanza amene akufuna moyo wanga.+

Sanaike Mulungu patsogolo pawo.+ [Seʹlah.]

 4 Taonani! Mulungu ndiye mthandizi wanga.+

Yehova ali pakati pa anthu amene akuchirikiza moyo wanga.

 5 Iye adzabwezera zoipa kwa adani anga.+

Achititseni kukhala chete chifukwa cha choonadi chanu.+

 6 Ndidzapereka nsembe kwa inu mofunitsitsa.+

Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu pakuti ndi labwino.+

 7 Pakuti anandilanditsa pa mavuto anga onse,+

Ndipo diso langa laona adani anga atagonja.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.

55 Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa.+

Musanyalanyaze pempho langa lakuti mundikomere mtima.+

 2 Ndimvetsereni mwatcheru ndi kundiyankha.+

Mtima wanga suli m’malo chifukwa cha mavuto anga,+

Sindingachitire mwina koma kusonyeza nkhawa zanga,

 3 Chifukwa cha zimene adani akunena, ndiponso chifukwa chakuti oipa andipanikiza.+

Pakuti akundikhuthulira mavuto,+

Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+

 4 Mtima wanga ukundipweteka kwambiri.+

Ndipo ndikuopa imfa.+

 5 Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera.+

Inde ndikunthunthumira.

 6 Ndipo ndikunena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!+

Ndikanauluka ndi kukakhala kwina.+

 7 Ndikanathawira kutali.+

Ndikanapita kukakhala m’chipululu.+ [Seʹlah.]

 8 Ndikanathawira kumalo opulumukirako,

Kuthawa mphepo yamphamvu, ndithu kuthawa mphepo yamkuntho.”+

 9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani zonena zawo,+

Pakuti ndaona ziwawa ndi mikangano mumzinda.+

10 Usana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.+

Ndipo mumzindawo muli zopweteka ndi masautso.+

11 Mmenemo muli mavuto okhaokha.

Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizinachoke kubwalo la mzindawo.+

12 Pakuti amene ananditonza si mdani.+

Akanakhala mdani ndikanapirira.

Amene anadzikweza pamaso panga si munthu wodana nane kwambiri.+

Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.+

13 Koma ndiwe, munthu wofanana ndi ine,+

Munthu amene ndimam’dziwa bwino ndiponso mnzanga weniweni,+

14 Chifukwa tinali mabwenzi apamtima.+

Tinali kuyenda limodzi ndi khwimbi la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.+

15 Chiwonongeko chiwagwere!+

Atsikire ku Manda ali amoyo.+

Pakuti kulikonse kumene apita, zinthu zoipa zimakhala mumtima mwawo.+

16 Koma ine ndidzafuulira Mulungu.+

Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+

17 Usiku, m’mawa ndi masana ndimakhala ndi nkhawa ndipo ndimakhala ndikulira,+

Choncho Mulungu amamva mawu anga.+

18 Iye adzandiwombola ndi kundikhazika pa mtendere, kundichotsa pankhondo,+

Pakuti khamu la anthu landiukira.+

19 Mulungu amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale,+

Adzandimvera ndipo adzawayankha,+ [Seʹlah.]

Anthu osafuna kusintha makhalidwe awo oipa,+

Ndiponso amene saopa Mulungu.+

20 Iye watambasula dzanja lake kuukira anthu amene ali naye pa mtendere.+

Wanyoza pangano lake.+

21 Mawu a pakamwa pake ndi osalala ngati mafuta a mkaka,+

Koma mtima wake umakonda ndewu.+

Mawu ake ndi osalala ngati mafuta,+

Koma ali ngati lupanga lakuthwa.+

22 Umutulire Yehova nkhawa zako,+

Ndipo iye adzakuchirikiza.+

Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.+

23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipa kumanda.+

Ndipo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso anthu achinyengo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+

Koma ine ndidzakhulupirira inu.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa “Nkhunda Yosanena Kanthu” pakati pa okhala kutali. Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+

56 Ndikomereni mtima inu Mulungu wanga, chifukwa munthu wopanda pake akufuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+

Akulimbana nane tsiku lonse ndi kundipondereza.+

 2 Tsiku lonse adani anga akufuna kundiwakha ndi pakamwa pawo,+

Pakuti anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.+

 3 Ine ndidzadalira inu, tsiku lililonse limene ndingachite mantha.+

 4 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu, ndidzatamanda mawu ake.+

Ine ndimadalira Mulungu, sindidzaopa.+

Kodi munthu angandichite chiyani?+

 5 Tsiku lonse amasokoneza zolinga zanga.

Nthawi zonse amaganiza zondichitira zoipa.+

 6 Amandiukira ndi kundibisalira,+

Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+

Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+

 7 Atayeni chifukwa cha zochita zawo zoipa.+

Inu Mulungu, gwetsani mitundu ya anthu mu mkwiyo wanu.+

 8 Inu mwalemba za kuthawathawa kwanga.+

Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa.+

Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?+

 9 Pa nthawi imeneyo adani anga adzabwerera pa tsiku limene ndidzaitana inu.+

Ndikudziwa bwino kuti Mulungu ali kumbali yanga.+

10 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu,+ ndidzatamanda mawu ake.

Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Yehova, ndidzatamanda mawu ake.+

11 Ine ndimadalira Mulungu. Sindidzaopa.+

Kodi munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+

12 Inu Mulungu, ine ndikuyenera kukwaniritsa malonjezo anga kwa inu.+

Ndidzapereka kwa inu nsembe zoyamikira.+

13 Pakuti inu mwalanditsa moyo wanga ku imfa.+

Inu mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe,+

Kuti ndiyendeyende pamaso pa Mulungu m’kuwala kumene kumaunikira anthu amoyo.+

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli n’kukalowa m’phanga.+

57 Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,+

Pakuti ine ndathawira kwa inu.+

Ndipo ndathawira mumthunzi wa mapiko anu kufikira masoka atadutsa.+

 2 Ndikufuulira Mulungu Wam’mwambamwamba, Mulungu woona amene akuthetsa masoka amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.+

 3 Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa.+

Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+ [Seʹlah.]

Mulungu adzasonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndi choonadi chake.+

 4 Moyo wanga uli pakati pa mikango.+

Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,

Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+

Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+

 5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+

Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+

 6 Iwo anditchera ukonde panjira yanga.+

Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni.+

Andikumbira mbuna.

Koma iwo agweramo.+ [Seʹlah.]

 7 Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+

Mtima wanga wakhazikika.

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani.+

 8 Iwe mtima wanga, galamuka.+

Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+

Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.

 9 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+

10 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+

Choonadi chanu chafika kuthambo.+

11 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+

Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.*

58 Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+

Kodi mungaweruze molungama, inu ana a anthu?+

 2 Ayi! Inu mukuchita zosalungama padziko lapansi mogwirizana ndi zimene mtima wanu ukufuna,+

Ndipo mukukonza njira zochitira chiwawa ndi manja anu.+

 3 Oipa akhala opotoka maganizo kuyambira ali m’mimba.+

Iwo asochera kuyambira ali m’mimba,

Ndipo amalankhula zabodza.+

 4 Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka,+

Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake,+

 5 Imene singamve mawu a munthu wamatsenga,+

Ngakhale wina wanzeru ataimanga ndi mphamvu zamatsenga.+

 6 Inu Mulungu, agululeni mano m’kamwa mwawo.+

Inu Yehova, thyolani nsagwada za mkango wamphamvu.

 7 Asungunuke ndi kupita ngati madzi.+

Mulungu akunge uta woponyera mivi yake pamene adaniwo akugwa.+

 8 Woipayo amayenda ngati nkhono imene ikusungunuka.

Iwo sadzaona dzuwa ngati mwana wa mayi amene wapita padera.+

 9 Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,+

Mulungu adzauluza ndi mphepo yamkuntho mitengo yaiwisi yaminga pamodzi ndi imene ikuyaka.+

10 Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+

Adzasambitsa mapazi ake m’magazi a anthu oipa.+

11 Ndipo mtundu wa anthu udzati:+ “Ndithudi wolungama adzalandira mphoto.+

Ndithudi pali Mulungu amene akuweruza dziko lapansi.”+

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu, ndipo anali kudikirira nyumba yake kuti amuphe.+

59 Inu Mulungu wanga, ndilanditseni kwa adani anga.+

Nditetezeni kwa anthu amene akundiukira.+

 2 Ndilanditseni kwa anthu ochita zopweteka anzawo,+

Ndipo ndipulumutseni kwa anthu amene ali ndi mlandu wa magazi.

 3 Pakuti, taonani! Iwo akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+

Inu Yehova, anthu amphamvu akundiukira,+

Ngakhale kuti ine sindinapanduke kapena kuchita tchimo lililonse.+

 4 Iwo akuthamanga ndi kukonzekera kundiukira, ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse.+

Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.+

 5 Inu Yehova, Mulungu wa makamu, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+

Nyamukani ndi kuweruza mitundu yonse ya anthu.+

Musakomere mtima aliyense woipa ndi wachiwembu.+ [Seʹlah.]

 6 Madzulo amabweranso.+

Ndipo amauwa ngati agalu+ ndi kuzungulira mzinda wonse.+

 7 Taonani! Amabwetuka ndi pakamwa pawo.+

Milomo yawo ili ngati malupanga,+

Pakuti iwo amati: “Ndani akumvetsera?”+

 8 Koma inu Yehova, mudzawaseka.+

Mudzanyoza mitundu yonse ya anthu.+

 9 Inu Mphamvu yanga, ndidzayang’anabe kwa inu.+

Pakuti Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+

10 Mulungu amene wandisonyeza kukoma mtima kosatha ndidzaonana naye maso ndi maso.+

Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga, adaniwo atagonja.+

11 Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga angaiwale.+

Ndi mphamvu zanu zochuluka achititseni kuyendayenda,+

Ndipo agwetseni, inu Yehova, chishango chathu,+

12 Chifukwa cha tchimo la pakamwa pawo, ndi mawu a pamilomo yawo.+

Agwidwe chifukwa cha kunyada kwawo,+

Chifukwa cha kutukwana ndi chinyengo zimene amachita mobwerezabwereza.

13 Afafanizeni mu mkwiyo wanu.+

Afafanizeni kuti asakhaleponso.

Ndipo adziwe kuti Mulungu akulamulira Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi.+ [Seʹlah.]

14 Asiyeni abwerenso madzulo.

Asiyeni auwe ngati agalu ndipo azungulire mzinda wonse.+

15 Asiyeni amenewo ayendeyende kufunafuna chakudya.+

Asakhute ndipo usiku asowe malo ogona.+

16 Koma ine, ndidzaimba za mphamvu yanu,+

M’mawa ndidzanena mosangalala za kukoma mtima kwanu kosatha.+

Pakuti inu mwakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+

Ndiponso malo anga othawirako pa nthawi ya masautso.+

17 Inu Mphamvu yanga, ine ndidzaimba nyimbo zokutamandani,+

Pakuti Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo, Mulungu wandisonyeza kukoma mtima kosatha.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Duwa la Chikumbutso. Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira.+ Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera ndi kukapha Aedomu 12,000 m’chigwa cha Mchere.+

60 Inu Mulungu, mwatitaya, ndipo mwasokoneza magulu athu ankhondo,+

Mwakwiya. Tiloleni tibwerere kwa inu.+

 2 Mwagwedeza dziko lapansi, ndipo mwaling’amba.+

Tsekani ming’alu yake, pakuti lagwedezeka.+

 3 Anthu anu mwawaonetsa zovuta.+

Mwatimwetsa vinyo ndipo tikuyenda dzandidzandi.+

 4 Anthu okuopani mwawapatsa chizindikiro+

Kuti athawe uta mokhotakhota. [Seʹlah.]

 5 Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+

Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kutiyankha.+

 6 Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+

“Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu ngati gawo la cholowa.+

Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+

 7 Giliyadi ndi wanga ndipo Manase ndi wanganso.+

Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.

Yuda ndi ndodo ya mtsogoleri wanga.+

 8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+

Ndidzaponyera Edomu nsapato zanga.+

Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+

 9 Ndani adzandibweretsa kumzinda wozunguliridwa ndi adani?+

Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+

10 Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+

Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+

11 Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+

Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+

12 Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+

Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide.

61 Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kochonderera.+

Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+

 2 Mtima wanga ukalefuka, ndidzafuulira inu, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+

Nditsogolereni ndi kundikweza pamwamba pa thanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+

 3 Pakuti inu mwakhala pothawirapo panga,+

Nsanja yolimba pamaso pa mdani.+

 4 Ndidzakhala mlendo m’chihema chanu mpaka kalekale.+

Ndidzathawira m’malo obisalamo kunsi kwa mapiko anu.+ [Seʹlah.]

 5 Pakuti inu Mulungu, mwamvetsera malonjezo anga.+

Mwandipatsa cholowa chimene mwasungira anthu oopa dzina lanu.+

 6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.+

Zaka zake zidzachuluka kufanana ndi mibadwo yambirimbiri.+

 7 Mfumuyo idzakhala pamaso pa Mulungu mpaka kalekale.+

Isonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha ndi kuipatsa choonadi kuti zimenezi ziiteteze.+

 8 Choncho ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka muyaya,+

Kuti ndikwaniritse malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide.

62 Ndithudi, moyo wanga ukuyembekezera Mulungu modekha.+

Chipulumutso changa chidzachokera kwa iye.+

 2 Iye ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+

Sindidzagwedezeka kwambiri.+

 3 Kodi mudzayesayesa kufikira liti kuti muphe munthu amene mumadana naye?+

Nonsenu muli ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene akulikankha kuti ligwe.+

 4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+

Bodza limawasangalatsa.+

Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]

 5 Ndithudi, yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga,+

Chifukwa chiyembekezo changa chichokera kwa iye.+

 6 Ndithudi, iye ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+

Sindidzagwedezeka.+

 7 Chipulumutso ndi ulemerero wanga zili mwa Mulungu.+

Iye ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+

 8 Mukhulupirireni nthawi zonse, anthu inu.+

Mukhuthulireni za mumtima mwanu.+

Mulungu ndiye pothawirapo pathu.+ [Seʹlah.]

 9 Ndithudi, ana a anthu ochokera kufumbi ali ngati mpweya,+

Ana a anthu ndi malo othawirako achinyengo.+

Onse pamodzi akaikidwa pasikelo ndi opepuka kuposa mpweya.+

10 Musadalire chizolowezi chobera ena mwachinyengo,+

Ndipo musakhale wachabechabe chifukwa chochita uchifwamba.+

Ngati chuma chanu chachuluka, mtima wanu wonse usakhale pachumacho.+

11 Kawiri konse ndamva kuti Mulungu wanena kuti,+

Mphamvu ndi za Mulungu.+

12 Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+

Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+

Nyimbo ya Davide pamene anali m’chipululu cha Yuda.+

63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+

Moyo wanga ukulakalaka inu.+

Thupi langa lalefuka chifukwa cholakalaka inu

M’dziko louma ndi lopanda chonde, lopanda madzi.+

 2 Choncho ndakuonani m’malo oyera,+

Chifukwa ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+

 3 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo,+

Milomo yanga idzakuyamikirani.+

 4 Choncho ndidzakutamandani pa nthawi yonse ya moyo wanga.+

Ndidzapemphera m’dzina lanu nditakweza manja anga.+

 5 Moyo wanga wakhutira ndi gawo labwino kwambiri, wakhutira ndi zinthu zabwino kwambiri,+

Ndipo milomo yanga ikukutamandani ndi mfuu yachisangalalo.+

 6 Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa,+

Pa nthawi za ulonda wa usiku* ndimasinkhasinkha za inu.+

 7 Pakuti mwandithandiza,+

Ndipo mumthunzi wa mapiko anu ndimafuula mosangalala.+

 8 Ndakulondolani kulikonse,+

Dzanja lanu lamanja landigwira mwamphamvu.+

 9 Koma ofuna kuwononga moyo wanga,+

Adzatsikira kumanda.+

10 Adzaphedwa ndi lupanga,+

Adzakhala chakudya cha nkhandwe.+

11 Ndipo mfumu idzakondwera mwa Mulungu.+

Aliyense wolumbira m’dzina la Mulungu adzam’tamanda,+

Pakuti pakamwa pa anthu olankhula chinyengo padzatsekedwa.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

64 Inu Mulungu, imvani mawu ofotokoza nkhawa zanga.+

Tetezani moyo wanga kuti usaope mdani.+

 2 Ndibiseni kuti ndisamve zinsinsi za anthu ochita zoipa,+

Kuti ndisamve phokoso la anthu ochita zovulaza anzawo,+

 3 Amene anola lilime lawo ngati lupanga,+

Amene alunjikitsa mivi yawo, imene ndi mawu awo owawa,+

 4 Pa munthu wosalakwa, kuti amulase atamubisalira.+

Amamulasa modzidzimutsa ndipo saopa.+

 5 Amaumirira kulankhula zoipa,+

Amakambirana kuti atchere misampha.+

Iwo amati: “Angaione ndani?”+

 6 Amafunafuna kuchita zinthu zosalungama,+

Abisa chiwembu chimene achikonza mochenjera,+

Ndipo zamkati, zamumtima mwa aliyense, n’zovuta kuzimvetsa.+

 7 Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi modzidzimutsa.+

Iwo adzakhala ndi zilonda,+

 8 Ndipo iwo amakhumudwitsa munthu,+

Koma lilime lawo likutsutsana nawo.+

Onse owayang’ana adzapukusa mitu yawo,+

 9 Anthu onse adzachita mantha,+

Ndipo adzanena za ntchito za Mulungu,+

Iwo adzamvetsa bwino ntchito zake.+

10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova ndipo adzathawira kwa iye,+

Ndipo onse owongoka mtima adzatamanda Mulungu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

65 Inu Mulungu, anthu akukutamandani mu Ziyoni+ ndipo akhala chete pamaso panu,

Iwo adzakwaniritsa malonjezo awo kwa inu.+

 2 Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+

 3 Zolakwa zanga zandikulira.+

Inu mudzatikhululukira* machimo athu.+

 4 Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu,+

Kuti akhale m’mabwalo anu.+

Tidzakhutira ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu,+

Malo anu oyera kapena kuti kachisi wanu woyera.+

 5 Mudzatiyankha ndi zinthu zochititsa mantha zochitika mwachilungamo,+

Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+

Inu Chidaliro cha malire onse a dziko lapansi ndi anthu okhala pafupi ndi nyanja zakutali.+

 6 Ndi mphamvu zake, iye akukhazikitsa mapiri,+

Iye wamanga mphamvu zochuluka m’chiuno mwake.+

 7 Iye akutontholetsa phokoso la nyanja,+

Akutontholetsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+

 8 Ndipo anthu okhala m’madera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu,+

Mudzachititsa kulowa ndi kutuluka kwa dzuwa kufuula mokondwera.+

 9 Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka,+

Mwalilemeretsa kwambiri.

Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wosefukira ndi madzi.+

Munalinganiza zinthu, kuti mbewu zawo zibale.+

Umu ndi mmene mumaperekera zinthu padziko lapansi.+

10 Mizere yawo imakhathamira, ndipo zibuma zake zimasalazidwa,+

Ndipo mumafewetsa nthaka ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera m’nthakayo.+

11 Mwaveka chaka chisoti chachifumu cha ubwino wanu,+

Ndipo njira zanu zikukha mafuta.+

12 Malo odyetserako ziweto a m’chipululu akukha mafuta,+

Ndipo zitunda zamangirira chisangalalo m’chiuno mwawo.+

13 Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,+

Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu.+

Malo onsewa akufuula mosangalala ndi kuimba chifukwa cha kupambana.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo.

66 Inu anthu nonse padziko lapansi, fuulirani Mulungu mosangalala chifukwa wapambana.+

 2 Imbani nyimbo zotamanda dzina lake.+

M’patseni ulemerero ndi kumutamanda.+

 3 Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+

Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zanu, adani anu adzabwera kwa inu mogonjera.+

 4 Anthu onse padziko lapansi adzakugwadirani,+

Ndipo adzaimba nyimbo zokutamandani, adzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ [Seʹlah.]

 5 Bwerani anthu inu, kuti muone ntchito za Mulungu.+

Zimene wachitira ana a anthu ndi zochititsa mantha.+

 6 Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+

Anthu anawoloka mtsinje mwa kuyenda ndi mapazi awo.+

Pamenepo tinayamba kusangalala mwa iye.+

 7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+

Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+

Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.]

 8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,+

Chititsani mawu omutamanda kumveka.+

 9 Iye amatisunga ndi moyo,+

Ndipo sanalole phazi lathu kupunthwa.+

10 Pakuti inu Mulungu mwatisanthula,+

Mwatiyenga ngati siliva.+

11 Mwatilowetsa mu ukonde wosakira nyama,+

Mwatinyamulitsa katundu wolemera m’chiuno mwathu.

12 Mwachititsa munthu wamba kutipondaponda.+

Tadutsa pamoto ndi pamadzi,+

Ndipo inu mwatipatsa mpumulo.+

13 Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza zathunthu.+

Ine ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu+

14 Amene milomo yanga inanena,+

Ndiponso amene pakamwa panga pananena nthawi imene ndinali m’masautso aakulu.+

15 Ndidzapereka kwa inu nsembe zathunthu zopsereza za nyama zonenepa,+

Pamodzi ndi nsembe zautsi wa nkhosa zamphongo.

Ndidzapereka ng’ombe yamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo.+ [Seʹlah.]

16 Bwerani, mvetserani, inu nonse oopa Mulungu, ndipo ine ndifotokoza+

Zimene wandichitira.+

17 Ndinamuitana ndi pakamwa panga,+

Ndipo ndinamutamanda ndi lilime langa.+

18 Ngati ndikuganizira choipa chilichonse mumtima mwanga,

Yehova sadzandimvera.+

19 Ndithudi, Mulungu wamva,+

Wamvetsera mwatcheru mawu a pemphero langa.+

20 Adalitsike Mulungu amene sananyalanyaze pemphero langa,

Kapena kundimana kukoma mtima kwake kosatha.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo.

67 Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa.+

Iye adzatikomera mtima,+ [Seʹlah.]

 2 Kuti njira zanu zidziwike padziko lapansi,+

Kuti chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse ya anthu.+

 3 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+

Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+

 4 Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+

Pakuti inu mudzaweruza anthu molungama.+

Ndipo mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. [Seʹlah.]

 5 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+

Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+

 6 Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.+

Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.+

 7 Mulungu adzatidalitsa,+

Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ndi Salimo.

68 Mulungu anyamuke,+ adani ake amwazike,+

Ndipo amene amadana naye kwambiri athawe pamaso pake.+

 2 Monga mmene mphepo imauluzira utsi, inunso muwauluze chimodzimodzi.+

Ngati mmene phula limasungunukira chifukwa cha moto,+

Anthu oipa awonongeke ndi kuchotsedwa pamaso pa Mulungu.+

 3 Koma olungama asangalale,+

Asekerere pamaso pa Mulungu,+

Ndipo akondwere ndi kusangalala.+

 4 Anthu inu, imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+

Muimbireni nyimbo Iye amene akudutsa m’chipululu,+

Amene dzina lake ndi Ya,*+ ndipo kondwerani pamaso pake.

 5 Tate wa ana amasiye* ndi woweruzira akazi amasiye milandu,+

Ndi Mulungu amene amakhala m’malo ake oyera.+

 6 Mulungu akuchititsa osungulumwa kukhala m’nyumba.+

Akumasula akaidi ndi kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+

Koma anthu osamvera adzakhala m’dziko lowonongeka ndi kutentha kwa dzuwa.+

 7 Inu Mulungu, pamene munatsogolera anthu anu,+

Pamene munadutsa m’chipululu,+ [Seʹlah.]

 8 Dziko lapansi linagwedezeka,+

Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+

Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+

 9 Inu Mulungu, munayamba kugwetsa mvula yamphamvu,+

Ngakhale pamene anthu anu anali ofooka, inu munawalimbitsa.+

10 Iwo anakhala mumsasa wanu wa mahema,+

Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino munakonzera munthu wosautsika msasa wa mahema.+

11 Yehova wapereka lamulo,+

Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.+

12 Mafumu enieniwo okhala ndi magulu a asilikali amathawa, ndithu amathawadi.+

Mkazi wongokhala pakhomo, nayenso amagwira nawo ntchito yofunkha.+

13 Ngakhale anthu inu mutagona pakati pa milu ya phulusa mumsasawo,

Mudzaona mapiko a njiwa okutidwa ndi siliva,

Ndipo nthenga za kumapeto a mapiko ake zidzakhala zagolide wobiriwira monkera ku chikasu.+

14 Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu a m’dzikomo,+

Mu Zalimoni+ munayamba kugwa chipale chofewa.

15 Dera lamapiri la ku Basana+ ndilo phiri la Mulungu.+

Dera lamapiri la ku Basana ndilo phiri la nsonga zitalizitali.+

16 N’chifukwa chiyani inu mapiri a nsonga zitalizitali mumayang’ana mwanjiru

Phiri limene Mulungu wafuna kukhalamo?+

Yehova adzakhala m’phiri limenelo mpaka muyaya.+

17 Magaleta ankhondo a Mulungu ali m’magulu a masauzande makumimakumi, ali m’magulu a masauzande osawerengeka.+

Yehova walowa m’malo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+

18 Mwakwera pamalo apamwamba,+

Mwatenga anthu ogwidwa,+

Mwatenga mphatso za amuna,+

Ndithu inu Yehova* Mulungu, mwatenga ngakhale anthu osamvera,+ kuti inu mukhale pakati pawo.+

19 Adalitsike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+

Mulungu woona wa chipulumutso chathu.+ [Seʹlah.]

20 Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+

Ndipo njira zopulumukira ku imfa ndi za Yehova,+ Ambuye Wamkulu Koposa.+

21 Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake kukhala zibenthuzibenthu,+

Adzaphwanya liwombo latsitsi la aliyense woyenda m’njira yochimwa.+

22 Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+

Ndidzawatulutsa m’nyanja yakuya,+

23 Kuti musambitse mapazi anu m’magazi,+

Kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.”+

24 Iwo aona magulu anu a anthu opambana akuyendera pamodzi, inu Mulungu,+

Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akukalowa kumalo oyera.+

25 Oimba nyimbo anali patsogolo, oimba zoimbira za zingwe anali pambuyo pawo,+

Pakati panali atsikana akuimba maseche.+

26 Pamisonkhano tamandani Mulungu,+

Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+

27 Pali fuko laling’ono la Benjamini limene likugonjetsa anthu,+

Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi makamu awo amene akufuula,

Palinso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafitali.+

28 Mulungu wanu walamula mphamvu zanu kuti zionekere.+

Inu Mulungu, sonyezani mphamvu monga mmene mwachitira kwa ife.+

29 Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+

Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+

30 Dzudzulani nyama yakutchire yokhala m’mabango,+ gulu la ng’ombe zamphongo,+

Pamodzi ndi mitundu ya anthu imene ili ngati ana a ng’ombe amphongo, aliyense amene akupondaponda ndalama zasiliva.+

Iye wabalalitsa mitundu ya anthu yokonda ndewu.+

31 Zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina* zidzabwera kuchokera ku Iguputo,+

Mwamsanga Kusi adzatambasula dzanja lake ndi kupereka mphatso kwa Mulungu.+

32 Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+

Imbani nyimbo zotamanda Yehova [Seʹlah.]

33 Imbirani Iye wokwera kumwamba kwa kumwamba kwakale.+

Tamverani! Iye akulankhula ndi mawu amphamvu.+

34 Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+

Iye akulamulira Isiraeli ndipo mphamvu zake zili m’mitambo.+

35 Mulungu akamatuluka m’malo ake opatulika aulemerero, amachititsa mantha.+

Iye ndi Mulungu wa Isiraeli, wopereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+

Mulungu adalitsike.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Salimo la Davide.

69 Ndipulumutseni, inu Mulungu, pakuti madzi afika m’khosi.+

 2 Ndamila m’matope akuya, mmene mulibe malo oponda.+

Ndalowa m’madzi akuya,

Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+

 3 Ndatopa ndi kufuula kwanga,+

Mawu asasa pammero panga.

Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+

 4 Anthu amene amadana nane popanda chifukwa achuluka kuposa tsitsi la m’mutu mwanga.+

Amene akufuna kunditsitsira kuli chete, chifukwa chodana nane popanda chifukwa, achuluka kwambiri.+

Ngakhale kuti sindine wakuba, anandikakamiza kubweza zinthu zimene zinabedwa.

 5 Inu Mulungu, mwadziwa kupusa kwanga,

Ndipo kupalamula kwanga sikunabisike kwa inu.+

 6 Onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,+

Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa makamu.+

Onse amene akufunafuna inu, asanyazitsidwe chifukwa cha ine,+

Inu Mulungu wa Isiraeli.+

 7 Ine ndanyamula chitonzo chifukwa cha inu,+

Manyazi aphimba nkhope yanga.+

 8 Ndadzipatula pakati pa abale anga,+

Ndipo ndakhala mlendo pakati pa ana aamuna a mayi anga.+

 9 Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya,+

Ndipo mnyozo wa anthu amene akukutonzani wagwa pa ine.+

10 Ndipo ndinalira ndi kusala kudya chifukwa cha moyo wanga,+

Koma anthu anali kungonditonza chifukwa cha zimenezo.+

11 Pamene ndinavala ziguduli,

Ndinakhala ngati mwambi kwa iwo.+

12 Anthu okhala kuchipata anayamba kundidera nkhawa,+

Ndipo anthu amene anali kumwa zakumwa zoledzeretsa anali kundinena mu nyimbo zawo.+

13 Koma ine ndinali kupemphera kwa inu Yehova,+

Pa nthawi yovomerezedwa, inu Mulungu.+

Ndiyankheni mwa kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha, ndipo sonyezani kuti ndinudi mpulumutsi.+

14 Ndipulumutseni m’matope kuti ndisamire.+

Ndipulumutseni kwa anthu odana nane+ ndiponso ku madzi akuya.+

15 Musalole kuti mtsinje wa madzi othamanga undikokolole,+

Kapena kuti madzi akuya andimize,

Kapenanso kuti dzenje* lindimeze ndi kutseka pakamwa pake.+

16 Ndiyankheni inu Yehova, pakuti kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwabwino.+

Ndicheukireni chifukwa chifundo chanu ndi chochuluka,+

17 Ndipo ine mtumiki wanu musandibisire nkhope yanu.+

Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndasautsika kwambiri.+

18 Yandikirani moyo wanga ndi kuupulumutsa.+

Ndiwomboleni kwa adani anga.+

19 Inu mwadziwa chitonzo changa, manyazi anga ndi kunyazitsidwa kwanga.+

Onse odana nane ali pamaso panu.+

20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+

Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+

Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+

21 Koma anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye,+

Ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.+

22 Tebulo lawo likhale msampha,+

Ndipo akodwe ndi chilichonse chimene akusangalala nacho.+

23 Maso awo achite mdima kuti asaone,+

Ndipo chititsani miyendo* yawo kunjenjemera mosalekeza.+

24 Atsanulireni matemberero anu,+

Ndipo mkwiyo woyaka moto uwagwere.+

25 Msasa wawo wokhala ndi mpanda ukhale bwinja,+

Ndipo m’mahema awo musapezeke munthu wokhalamo.+

26 Pakuti iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,+

Ndipo amakamba za ululu wa anthu amene inu mwawalasa.

27 Wonjezerani zolakwa pa zolakwa zawo,+

Ndipo inu musawaone monga olungama.+

28 Afafanizidwe m’buku la anthu amoyo,+

Ndipo iwo asalembedwe m’bukumo pamodzi ndi anthu olungama.+

29 Koma ine ndasautsika ndipo ndikumva kupweteka.+

Inu Mulungu, chipulumutso chanu chinditeteze.+

30 Ndidzatamanda dzina la Mulungu mwa kuimba nyimbo,+

Ndipo ndidzamulemekeza ndi nyimbo zomuyamika.+

31 Zimenezinso zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ng’ombe yamphongo,+

Kuposa ng’ombe yamphongo yaing’ono imene ili ndi nyanga, komanso yogawanika ziboda.+

32 Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+

Inu amene mukutumikira Mulungu, mtima wanu ukhalenso ndi moyo.+

33 Pakuti Yehova akumvetsera osauka,+

Ndipo sadzanyoza anthu ake amene ali m’ndende.+

34 Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+

Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo.+

35 Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,+

Ndipo adzamanga mizinda ya Yuda,+

Iwo adzakhala mmenemo ndi kutenga dzikolo kukhala lawo.+

36 Ana a atumiki ake adzalandira dzikolo monga cholowa chawo,+

Ndipo anthu okonda dzina lake adzakhala mmenemo.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.+

70 Inu Mulungu, fulumirani kundilanditsa,+

Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+

 2 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+

Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+

 3 Amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!” abwerere chifukwa cha manyazi awo.+

 4 Onse amene akufunafuna inu akondwere ndi kusangalala mwa inu,+

Ndipo onse amene amakonda chipulumutso chanu, nthawi zonse azinena kuti: “Mulungu alemekezeke!”+

 5 Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+

Inu Mulungu, chitanipo kanthu mwamsanga kuti zinthu zindiyendere bwino.+

Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+

Inu Yehova musachedwe.+

71 Inu Yehova, ine ndathawira kwa inu.+

Musalole kuti ndichite manyazi.+

 2 Mundilanditse chifukwa cha chilungamo chanu ndipo mundipulumutse.+

Tcherani khutu lanu kwa ine ndi kundipulumutsa.+

 3 Mukhale thanthwe lachitetezo loti ndizilowamo nthawi zonse.+

Lamulani kuti ndipulumutsidwe,+

Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+

 4 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni m’manja mwa woipa,+

Ndipulumutseni m’manja mwa munthu wochita zinthu mopanda chilungamo komanso mopondereza.+

 5 Pakuti chiyembekezo changa ndinu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndimadalira inu kuyambira pa unyamata wanga.+

 6 Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga inu mwandithandiza.+

Inu ndi amene munanditulutsa m’mimba mwa mayi anga.+

Ndimatamanda inu nthawi zonse.+

 7 Ndakhala ngati chozizwitsa kwa anthu ambiri,+

Koma inu ndinu malo anga olimba othawirako.+

 8 M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+

Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+

 9 Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga.+

Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.+

10 Pakuti adani anga anena za ine,+

Ndipo anthu olondalonda moyo wanga, onse pamodzi achita upo,+

11 Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya.+

Mulondoleni ndi kumugwira pakuti palibe womulanditsa.”+

12 Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.+

Inu Mulungu wanga, fulumirani kundithandiza.+

13 Anthu otsutsana nane achite manyazi, iwo awonongedwe.+

Amene akufunafuna kundigwetsera tsoka adziphimbe ndi chitonzo ndiponso manyazi.+

14 Koma ine ndidzayembekezera inu nthawi zonse,+

Ndipo ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale.

15 Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+

Padzanena za chipulumutso chanu tsiku lonse,+

Pakuti ntchito za chilungamo ndi chipulumutso chanu ndi zochuluka ndipo sindinathe kuziwerenga.+

16 Ndidzabwera ndi kunena za mphamvu zanu zazikulu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+

Ndidzanena za chilungamo chanu, osati cha wina aliyense.+

17 Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga,+

Ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa.+

18 Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+

Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+

Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+

19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+

Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+

Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+

20 Chifukwa chakuti mwandionetsa masautso ndi masoka ambiri,+

Nditsitsimutseni.+

Nditulutseninso m’madzi akuya, pansi pa nthaka.+

21 Kulitsani ulemu wanga,+

Mundizungulire ndi chitetezo chanu ndi kundilimbikitsa.+

22 Inenso ndidzakutamandani ndi chipangizo cha zingwe,+

Ndidzatamanda choonadi chanu, inu Mulungu.+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi zeze, Inu Woyera wa Isiraeli.+

23 Ndikafuna kuimba nyimbo zokutamandani, pakamwa panga padzafuula mokondwera,+

Ngakhalenso moyo wanga umene mwauwombola+ udzakutamandani.

24 Ngakhalenso lilime langa lidzalankhula chapansipansi za chilungamo chanu tsiku lonse,+

Pakuti ofunafuna kundigwetsera tsoka achita manyazi ndipo athedwa nzeru.+

Salimo lonena za Solomo.

72 Inu Mulungu, dziwitsani mfumu za zigamulo zanu,+

Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+

 2 Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+

Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+

 3 Mapiri atenge mtendere ndi kupita nawo kwa anthu,+

Komanso zitunda zitenge mtendere wopezeka mwachilungamo.

 4 Aweruze osautsika pakati pa anthu,+

Apulumutse ana a anthu osauka,

Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.

 5 Iwo adzakuopani nthawi zonse pamene dzuwa likuwala,+

Adzakuopani ku mibadwomibadwo pamene mwezi uli kuthambo.+

 6 Adzatsika ngati mvula pa udzu umene wadulidwa,+

Ngati mvula yambiri yamvumbi imene imanyowetsa kwambiri nthaka.+

 7 M’masiku ake, wolungama adzaphuka,+

Ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.+

 8 Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+

Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+

 9 Anthu okhala m’madera opanda madzi adzagwada pamaso pake,+

Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+

10 Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+

Adzapereka msonkho.+

Mafumu a ku Sheba ndi Seba

Adzapereka mphatso.+

11 Mafumu onse adzamugwadira ndi kumuweramira.+

Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.+

12 Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,+

Komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.+

13 Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,+

Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.+

14 Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa,

Ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.+

15 Iye akhale ndi moyo wautali,+ ndipo apatsidwe wina mwa golide wa ku Sheba.+

Nthawi zonse anthu azimupempherera.

Adalitsike tsiku lililonse.+

16 Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+

Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.+

Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+

Ndipo anthu ochokera mumzinda adzaphuka ngati udzu wa panthaka.+

17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+

Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka,

Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+

Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+

18 Adalitsike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+

Iye yekha amene akuchita ntchito zodabwitsa.+

19 Lidalitsike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+

Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+

Ame! Ame!*

20 Mapemphero a Davide mwana wa Jese,+ athera pamenepa.

BUKU LACHITATU

(Masalimo 73 – 89)

Nyimbo ya Asafu.+

73 Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+

 2 Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka,+

Mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.+

 3 Pakuti ndinachitira nsanje anthu odzitukumula,+

Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+

 4 Pakuti samva zowawa za imfa.+

Ndipo mimba zawo ndi zazikulu chifukwa cha kunenepa.+

 5 Iwo sakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo,+

Ndipo sakumana ndi masoka mofanana ndi anthu ena onse.+

 6 Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda m’khosi mwawo,+

Ndipo avala chiwawa ngati malaya.+

 7 Diso lawo latuzuka chifukwa cha kunenepa.+

Achita zambiri kuposa zolingalira za mtima wawo.+

 8 Iwo amanyodola ndi kulankhula zinthu zoipa.+

Amalankhula za chinyengo chawo modzikweza.+

 9 Kudzikweza kwawo kwafika kumwamba,+

Akuyendayenda padziko lapansi ndipo lilime lawo likunena zilizonse zimene akufuna.+

10 Choncho woipa amatengera anthu a Mulungu kumalo omwewo,

Ndipo amamwa madzi m’kapu yodzaza bwino.

11 Iwo anena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+

Kodi Wam’mwambamwamba akudziwa zimenezi?”+

12 Onani! Awa ndi anthu oipa, amene akukhala mosatekeseka mpaka kalekale.+

Iwo achulukitsa chuma chawo.+

13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,+

Ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.+

14 Ndinali kukumana ndi masoka tsiku lililonse,+

Ndipo m’mawa uliwonse ndinali kudzudzulidwa.+

15 Ngati ndikananena kuti: “Ndidzalankhula za zinthu zimenezi,”

Pamenepo ndikanachitira chinyengo

M’badwo wa ana anu aamuna.+

16 Ndipo ndinali kuganizira nkhani imeneyi kuti ndiimvetse.+

Zinali zopweteka kwa ine,

17 Kufikira pamene ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.+

Ndinafuna kudziwa za tsogolo lawo.+

18 Ndithudi, mwawaimika pamalo oterera.+

Mwawagwetsa kuti awonongeke.+

19 Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+

Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa!

20 Inu Yehova, anthu amenewa ali ngati maloto amene aiwalika podzuka.+

Choncho pamene mukuimirira mudzawakana mochititsa manyazi.+

21 Pakuti mtima unandipweteka+

Ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.+

22 Ndinakhala wopanda nzeru ndipo sindinadziwe kanthu.+

Ndinakhala ngati nyama yakuthengo pamaso panu.+

23 Koma ine ndili ndi inu nthawi zonse.+

Mwandigwira dzanja langa lamanja.+

24 Mudzanditsogolera ndi malangizo anu,+

Ndipo pambuyo pake mudzanditenga ndi kundipatsa ulemerero.+

25 Winanso ndani kumwambako amene ali kumbali yanga?+

Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.+

26 Thupi langa ndi mtima wanga zalefuka.+

Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+

27 Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+

Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+

28 Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+

Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga,+

Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Masikili.* Salimo la Asafu.+

74 Inu Mulungu, n’chifukwa chiyani mwatitaya?+

N’chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira nkhosa zimene mukuweta?+

 2 Kumbukirani anthu amene munawatenga kukhala anu kalelo,+

Fuko limene munaliwombola monga cholowa chanu,+

Ndi phiri la Ziyoni ili mmene inu mukukhala.+

 3 Pitani kumalo amene awonongedwa.+

M’malo oyera, mdani wachitira zoipa china chilichonse.+

 4 Anthu amene akukuchitirani zoipa afuula mosangalala kuti apambana m’malo anu olambiriramo.+

Aikamo mbendera zawo monga zizindikiro.+

 5 Iwo amatchuka ngati munthu amene amagwetsa mitengo ndi nkhwangwa m’nkhalango.

 6 Ndipo tsopano zojambula mochita kugoba za m’makoma a malo opatulika, onse amazichotsa ndi nkhwangwa komanso ndodo zokhala ndi chitsulo kumutu kwake.+

 7 Iwo atentha malo anu opatulika.+

Aipitsa ndi kugwetsera pansi chihema chokhala ndi dzina lanu.+

 8 Iwo, ngakhalenso ana awo, onse pamodzi anena mumtima mwawo kuti:

“Malo onse olambiriramo a Mulungu ayenera kutenthedwa m’dzikoli.”+

 9 Zizindikiro zathu sitinazione, ndipo palibenso mneneri amene watsala,+

Pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zikhala choncho mpaka liti.

10 Inu Mulungu, kodi mdani adzakuchitirani mopanda ulemu kufikira liti?+

Kodi mdani adzanyoza dzina lanu kwamuyaya?+

11 N’chifukwa chiyani mwachotsa dzanja lanu, dzanja lanu lamanja,+

Pachifuwa panu koma osachitapo kanthu? Kodi mukatero ife sitiwonongedwa?

12 Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,+

Iye ndiye wondipatsa chipulumutso chachikulu padziko lapansi.+

13 Inu munavundula nyanja ndi mphamvu zanu.+

Pakati pa madzi munadula mitu ya zilombo za m’nyanja.+

14 Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani*+ kukhala zidutswazidutswa.

Munaipereka kwa anthu monga chakudya, munaipereka kwa anthu okhala m’madera opanda madzi.+

15 Ndinu amene munang’amba nthaka ndi kupanga akasupe ndi makwawa.+

Inu munaumitsa mitsinje imene inali kukhala ndi madzi nthawi zonse.+

16 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu.+

Inu munapanga chounikira, munapanga dzuwa.+

17 Ndinu amene munaika malire onse a dziko lapansi.+

Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+

18 Kumbukirani izi: Inu Yehova, mdani wakuchitirani mopanda ulemu,+

Ndipo anthu opusa anyoza dzina lanu.+

19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo chakuthengo.+

Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu osautsika.+

20 Kumbukirani pangano limene munachita nafe,+

Pakuti malo a mdima a dziko lapansi adzaza ndi chiwawa.+

21 Musalole kuti munthu woponderezedwa achite manyazi.+

Munthu wosautsika ndi wosauka atamande dzina lanu.+

22 Nyamukani inu Mulungu, weruzani mlandu wanu.+

Kumbukirani mmene munthu wopusa wakunyozerani tsiku lonse.+

23 Musaiwale mawu a anthu amene akukuchitirani zoipa.+

Phokoso la anthu okuukirani likukwera kumwamba nthawi zonse.+

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

75 Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani,+

Ndipo dzina lanu lili pafupi ndi ife.+

Anthu ayenera kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+

 2 Mulungu akuti:* “Ndinasankha nthawi yoikidwiratu,+

Ndipo ndinayamba kuweruza mwachilungamo.+

 3 Dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo anayamba kusungunuka chifukwa cha mantha,+

Ndine amene ndinakonzanso zipilala zake.”+ [Seʹlah.]

 4 Anthu opusa ndinawauza kuti: “Musakhale opusa,”+

Ndipo oipa ndinawauza kuti: “Musakweze nyanga.*+

 5 Musakweze nyanga yanu pamwamba.

Musalankhule modzikuza.+

 6 Pakuti kukwezeka kwa munthu sikuchokera kum’mawa,

Kumadzulo kapena kum’mwera.

 7 Mulungu ndiye woweruza.+

Amatsitsa wina ndi kukweza wina.+

 8 M’dzanja la Yehova muli kapu.+

Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu.

Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake.

Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+

 9 Koma ine ndidzasimba zimenezi mpaka kalekale.

Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.+

10 Mulungu akuti:* “Ndidzadula nyanga zonse za anthu oipa.”+

Koma nyanga za munthu wolungama zidzakwezedwa.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

76 Mulungu amadziwika mu Yuda.+

Dzina lake ndi lalikulu mu Isiraeli.+

 2 Malo ake opumulirako ali ku Salemu,+

Malo ake okhalamo ali ku Ziyoni.+

 3 Kumeneko wathyola mivi yoyaka moto,+

Wathyola chishango, lupanga ndi zida zankhondo.+ [Seʹlah.]

 4 Inu Mulungu, mwazunguliridwa ndi kuwala, ndipo ndinu wochititsa nthumanzi kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.+

 5 Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo,+

Iwo awodzera ndi kugona tulo,+

Ndipo palibe ngakhale mmodzi mwa anthu onse olimba mtimawo amene ali ndi mphamvu zotsutsa.+

 6 Hatchi komanso wokwera galeta agona tulo tofa nato chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo.+

 7 Inu ndinu wochititsa mantha,+

Ndani angaime pamaso panu inu mutakwiya kwambiri?+

 8 Munachititsa ziweruzo zanu kumveka kuchokera kumwambako.+

Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala duu+

 9 Pamene Mulungu ananyamuka ndi kupereka chiweruzo,+

Kuti apulumutse anthu onse ofatsa padziko lapansi.+ [Seʹlah.]

10 Pakuti mkwiyo wa munthu udzakutamandani,+

Mkwiyo wake wotsala mudzaumangirira m’chiuno mwanu.

11 Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+

Bweretsani mphatso mwamantha.+

12 Mulungu adzatsitsa atsogoleri odzikuza.+

Iye ndi wochititsa mantha kwa mafumu a padziko lapansi.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

77 Ndidzafuulira Mulungu,+

Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzatchera khutu lake kwa ine.+

 2 Pa tsiku la zowawa zanga ndafunafuna Yehova.+

Ndakweza dzanja langa kumwamba usiku wonse, ndipo silinachite dzanzi.

Koma sindinatonthozeke.+

 3 Ndidzakumbukira Mulungu ndipo ndidzavutika maganizo.+

Ine ndasautsika. N’chifukwa chake ndafooka.+ [Seʹlah.]

 4 Mwatsegula zikope zanga,+

Ndipo ndavutika mtima, moti sindingathe kulankhula.+

 5 Ndaganizira za masiku akale,+

Ndaganizira zaka za makedzana.

 6 Usiku ndidzakumbukira nyimbo zanga zoimbidwa ndi chipangizo cha zingwe.+

Ndidzasonyeza kudera nkhawa mumtima mwanga,+

Ndipo ndidzasinkhasinkha zinthu zonse mozama.

 7 Kodi Yehova watitaya mpaka kalekale?+

Kodi sitidzathanso kumusangalatsa?+

 8 Kodi kukoma mtima kwake kosatha wakusiya mpaka muyaya?+

Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa+ ku mibadwomibadwo?

 9 Kodi Mulungu waiwala kukhala wokoma mtima,+

Kapena watsekereza chifundo chake mwaukali?+ [Seʹlah.]

10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundisautsa n’zakuti,+

Wam’mwambamwamba wasiya kutipatsa thandizo”?+

11 Ndidzakumbukira zochita za Ya,+

Ndithu ndidzakumbukira ntchito yanu yodabwitsa yakale.+

12 Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse,+

Ndipo ndiziganizira zochita zanu.+

13 Inu Mulungu, njira yanu ili m’malo oyera.+

Kodi ndi Mulungu wamkulu uti amene angafanane ndi Mulungu wathu?+

14 Inu ndinu Mulungu woona amene mukuchita zodabwitsa.+

Mphamvu zanu mwazidziwikitsa pakati pa mitundu ya anthu.+

15 Ndi dzanja lanu mwawombola anthu anu,+

Ana aamuna a Yakobo ndi Yosefe. [Seʹlah.]

16 Madzi akuonani, inu Mulungu,

Madzi akuonani, ndipo ayamba kumva ululu woopsa.+

Komanso madzi akuya ayamba kuwinduka.+

17 Mitambo yatulutsa mabingu ndi kugwetsa madzi.+

Thambo latulutsa mkokomo.

Mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+

18 Phokoso la bingu lanu linali ngati la mawilo a galeta.+

Mphezi zinaunika padziko.+

Ndipo dziko lapansi linagwedezeka ndi kuyamba kunjenjemera.+

19 Msewu wanu unadutsa panyanja,+

Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri.

Mmene mapazi anu anaponda simunaoneke.

20 Mwatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+

Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+

Masikili.* Salimo la Asafu.+

78 Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.+

Tcherani khutu ku mawu a pakamwa panga.+

 2 Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mwambi.+

Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale,+

 3 Amene tinamva ndipo tikuwadziwa,+

Komanso amene makolo athu anatifotokozera.+

 4 Mbadwa zawo sitikuzibisira mawu ophiphiritsawa,+

Ndipo tidzawasimba ngakhale ku mibadwo ya m’tsogolo.+

Tidzasimba ntchito zotamandika za Yehova ndi mphamvu zake,+

Komanso zinthu zodabwitsa zimene wachita.+

 5 Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,+

Iye anaika chilamulo mu Isiraeli,+

Zinthu zimene analamula makolo athu,+

Kuti auze ana awo.+

 6 Kuti m’badwo wa m’tsogolo, ana amene adzabadwe m’tsogolo, adzadziwe zimenezi,+

Kuti nawonso adzanyamuke ndi kusimbira ana awo.+

 7 Kuti anawo azidzadalira Mulungu,+

Ndi kuti asadzaiwale zochita za Mulungu+ koma kuti azidzasunga malamulo ake.+

 8 Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,+

M’badwo wosamva ndi wopanduka,+

M’badwo umene sunakonze mtima wawo,+

Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.+

 9 Ana a Efuraimu, ngakhale kuti anali ndi mivi ndi mauta,+

Anathawa pa tsiku lankhondo.+

10 Iwo sanasunge pangano la Mulungu,+

Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake.+

11 Iwo anayambanso kuiwala zochita zake,+

Ndi ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+

12 Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awo+

M’dziko la Iguputo,+ m’dera la Zowani.+

13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,+

Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma.+

14 Iye anapitiriza kuwatsogolera ndi mtambo masana,+

Ndipo usiku wonse anali kuwatsogolera ndi kuwala kwa moto.+

15 Iye anang’amba miyala m’chipululu+

Kuti awapatse madzi akumwa ochuluka ngati a m’nyanja.+

16 Iye anatulutsa madzi ambiri pathanthwe,+

Ndipo anachititsa madzi kutsika ngati mitsinje.+

17 Koma iwo anapitiriza kumuchimwira+

Mwa kupandukira Wam’mwambamwamba m’dera lopanda madzi.+

18 Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+

Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka.+

19 Pamenepo anayamba kulankhula mawu oipa kwa Mulungu.+

Iwo anati: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m’chipululu muno?”+

20 Taonani! Kodi Mulungu si uja anamenya thanthwe+

Kuti madzi atuluke, kutinso patuluke mitsinje yodzaza madzi?+

Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,+

Kapena kodi angakonzere anthu ake chakudya?”+

21 Choncho Yehova anamva zimenezo ndipo anakwiya.+

Moti moto unayakira Yakobo,+

Ndipo mkwiyo unatsikira pa Isiraeli.+

22 Pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu.+

Sanakhulupirire kuti iye adzawapulumutsa.+

23 Pamenepo Mulungu analamula mitambo ya m’mlengalenga,

Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba.+

24 Ndipo anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.+

Iye anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+

25 Anthu anadya chakudya cha amphamvu.+

Iye anawatumizira chakudya chokwanira.+

26 Anachititsa mphepo ya kum’mawa kuwomba m’mlengalenga,+

Ndipo mwa mphamvu zake anachititsa mphepo ya kum’mwera kuwomba.+

27 Iye anagwetsa chakudya pa iwo ngati fumbi.+

Anawagwetsera zolengedwa zamapiko zouluka, zochuluka ngati mchenga wakunyanja.+

28 Anapitiriza kuwagwetsera zimenezi mumsasa wake,+

Kuzungulira mahema ake onse.+

29 Iwo anadya ndi kukhuta kwambiri.+

Iye anawabweretsera zimene anali kulakalaka.+

30 Iwo anafunabe chakudya china,

Pamene china chinali m’kamwa.+

31 Nthawi yomweyo, mkwiyo wa Mulungu unatsikira pa iwo.+

Iye anayamba kupha anthu awo amphamvu.+

Ndipo anakomola anyamata a mu Isiraeli.

32 Ngakhale zinali choncho, iwo anawonjezera machimo awo,+

Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+

33 Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+

Anadula zaka za moyo wawo ndi masoka.

34 Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo anali kumufunafuna.+

Anali kutembenuka ndi kuyamba kufunafuna Mulungu.+

35 Iwo anali kukumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+

Ndiponso kuti Mulungu Wam’mwambamwamba anali Wowabwezerera.+

36 Koma iwo anali kufuna kum’pusitsa ndi pakamwa pawo.+

Ndi lilime lawo anali kufuna kunena bodza kwa iye.+

37 Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.+

Ndipo iwo sanakhulupirike ku pangano lake.+

38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+

Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+

Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.

39 Iye anali kukumbukira nthawi zonse kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+

Anali kukumbukira kuti moyo wawo umachoka ndipo subwereranso.+

40 Iwo analitu kumupandukira kawirikawiri m’chipululu,+

Anali kumukhumudwitsa m’chipululumo!+

41 Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu,+

Ndipo anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.+

42 Iwo sanakumbukire dzanja la Mulungu,+

Sanakumbukire tsiku limene anawawombola kwa mdani wawo,+

43 Iwo sanakumbukire mmene anaikira zizindikiro zake mu Iguputo,+

Ndi zozizwitsa zimene anachita m’dera la Zowani,+

44 Mmene anasinthira mitsinje ing’onoing’ono yotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+

Moti sanathe kumwa madzi ake.+

45 Mulungu anawatumizira tizilombo toyamwa magazi kuti tiwadye,+

Ndi achule kuti awawononge.+

46 Anapereka zokolola zawo kwa mphemvu,

Ndipo ntchito yawo yolemetsa anaipereka kwa dzombe.+

47 Anapha mitengo yawo ya mpesa ndi mvula yamatalala.+

Anapha mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala.+

48 Anaphanso nyama zawo zonyamula katundu ndi matalala,+

Ndiponso ziweto zawo ndi mliri wakupha.

49 Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,+

Ukali, ziweruzo zamphamvu ndi masautso.+

Anawatumizira makamu a angelo obweretsa masoka.+

50 Mkwiyo wake anaulambulira njira.+

Sanawabweze kuwachotsa ku imfa.

Ndipo anawapha ndi mliri.+

51 Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa mu Iguputo,+

Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka m’mahema a Hamu.+

52 Kenako anachititsa anthu ake kuchoka m’dzikolo ngati gulu la nkhosa,+

Anawayendetsa m’chipululu ngati gulu la ziweto.+

53 Anapitiriza kuwatsogolera ndi kuwateteza ndipo iwo sanachite mantha.+

Nyanja inamiza adani awo.+

54 Kenako anawalowetsa m’dziko lake lopatulika,+

M’dera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+

55 Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,+

Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,+

Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo.+

56 Koma iwo anayamba kuyesa Mulungu Wam’mwambamwamba ndi kum’pandukira,+

Ndipo sanasunge zikumbutso zake.+

57 Iwo anali kubwerera ndi kuchita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+

Anapotoka maganizo ngati uta wosakunga kwambiri.+

58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+

Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+

59 Mulungu anamva+ ndipo anakwiya kwambiri.+

Chotero ananyansidwa kwambiri ndi Isiraeli.+

60 Pamapeto pake anasiya chihema chopatulika cha ku Silo,+

Hema limene anali kukhalamo pakati pa anthu ochokera kufumbi.+

61 Analola kuti chizindikiro cha mphamvu zake chitengedwe ndi adani ake,+

Iye analola kuti chizindikiro cha kukongola kwake chikhale m’manja mwa adani.+

62 Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+

Ndipo anakwiyira cholowa chake.+

63 Anyamata ake ananyeka ndi moto,

Ndipo anamwali ake sanatamandidwe.+

64 Ansembe ake anagwa ndi lupanga,+

Ndipo akazi awo amasiye sanalire.+

65 Pamenepo Yehova anagalamuka ngati akudzuka kutulo,+

Ngati munthu wamphamvu amene akugalamuka pambuyo pomwa vinyo wambiri.+

66 Iye anathamangitsa adani ake ndi kuwapha.+

Anawachititsa kuti akhale akutonzedwa mpaka kalekale.+

67 Iye anakana hema wa Yosefe,+

Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu.+

68 Koma anasankha fuko la Yuda,+

Phiri la Ziyoni limene analikonda.+

69 Anayamba kumanga malo opatulika ngati malo okwera a paphiri,+

Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+

70 Choncho anasankha Davide mtumiki wake,+

Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa.+

71 Anamutenga kumene anali kuweta nkhosa zoyamwitsa,+

Anamutenga kuti akhale m’busa wa ana a Yakobo amene ndi anthu ake,+

Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake.+

72 Iye anayamba kuwaweta malinga ndi mtima wake wosagawanika,+

Ndipo anayamba kuwatsogolera mwaluso.+

Nyimbo ya Asafu.

79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa m’dziko limene ndilo cholowa chanu.+

Aipitsa kachisi wanu woyera.+

Awononga Yerusalemu ndi kumusandutsa bwinja.+

 2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+

Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+

 3 Atsanula magazi awo ngati madzi

Kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wowaika m’manda.+

 4 Anthu oyandikana nafe akutitonza,+

Anthu otizungulira akutinyoza ndi kutiseka.+

 5 Haa! Inu Yehova, mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+

Kodi mkwiyo wanu udzakhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+

 6 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+

Ndi pa maufumu amene sakuitana pa dzina lanu.+

 7 Pakuti iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo,+

Ndipo malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+

 8 Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+

Fulumirani! Tisonyezeni chifundo chanu,+

Chifukwa tasautsika koopsa.+

 9 Tithandizeni inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+

Kuti dzina lanu lilemekezedwe.+

Tipulumutseni ndi kutikhululukira* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+

10 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+

Pamene mukubwezera anthu a mitundu inawo chifukwa cha magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa,+

Ife tidzaone ndi maso athu.+

11 Mverani kuusa moyo kwa mkaidi.+

Anthu opita kukaphedwa muwateteze ndi dzanja lanu lamphamvu.+

12 Bwezerani anthu oyandikana nafe mwa kuwatsanulira chitonzo pachifuwa pawo maulendo 7,+

Inu Yehova, muwabwezere chitonzo chimene anachita pa inu.+

13 Koma ife, anthu anu, nkhosa zimene mukuweta,+

Tidzakuyamikani mpaka kalekale.

Tidzakutamandani ku mibadwomibadwo.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Chikumbutso.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

80 Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+

Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+

Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+

 2 Sonyezani mphamvu zanu pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase,+

Ndipo bwerani mudzatipulumutse.+

 3 Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+

Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+

 4 Inu Yehova Mulungu wa makamu, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?+

 5 Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,+

Ndipo mukuwamwetsabe misozi yochuluka kwambiri.+

 6 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azimenyana polimbirana ifeyo.+

Ndipo adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+

 7 Inu Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+

Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+

 8 Munachititsa mtengo wa mpesa kuchoka mu Iguputo.+

Munapitikitsa mitundu ya anthu kuti mubzalemo mtengowo.+

 9 Munalambula malo obzalapo mtengo wa mpesawo+ kuti uzike mizu ndi kudzaza dziko.+

10 Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake,

Ndipo mikungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.+

11 Pang’onopang’ono nthambi zake zinafika kunyanja,+

Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.*+

12 N’chifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wake wamiyala?+

Ndipo n’chifukwa chiyani anthu onse odutsa mumsewu akuthyola zipatso zake?+

13 Nguluwe ikuwononga mtengowo,+

Ndipo magulu a nyama zakutchire akuudya.+

14 Inu Mulungu wa makamu, chonde bwererani.+

Yang’anani pansi pano muli kumwambako, ndipo onani ndi kusamalira mtengo wa mpesa uwu.+

15 Onani muzu umene dzanja lanu lamanja linabzala.+

Muonenso mwana wanu amene munamulimbitsa kuti inu mulemekezeke.+

16 Watenthedwa ndi moto ndi kudulidwa.+

Iwo amawonongeka ndi kudzudzula kwa pankhope panu.+

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa kudzanja lanu lamanja,+

Ndipo likhale pa mwana wa munthu amene mwamulimbitsa kuti mulemekezeke.+

18 Ndipo ife sitidzabwerera kukusiyani.+

Tisungeni amoyo kuti tiitane pa dzina lanu.+

19 Inu Yehova Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+

Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Salimo la Asafu.

81 Anthu inu, fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu,+

Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.+

 2 Yambani kuimba nyimbo+ ndipo tengani maseche,+

Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.+

 3 Pa tsiku lokhala mwezi, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+

Pa tsiku looneka mwezi wathunthu, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, loimba pa tsiku la chikondwerero.+

 4 Pakuti limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,+

Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.

 5 Anaika chigamulocho monga chikumbutso kwa Yosefe,+

Pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+

Ndinali kumva chilankhulo chimene sindinali kuchidziwa.+

 6 Mulungu akuti: “Ndinachotsa goli paphewa lake.+

Manja ake anamasuka ndipo sananyamule dengu.+

 7 Pa nthawi ya nsautso unaitana ndipo ine ndinakupulumutsa.+

Ndinayamba kukuyankha m’malo obisika a bingu.+

Ndinakusanthula pamadzi a Meriba.+ [Seʹlah.]

 8 Imvani anthu anga, ndipo ndidzakulangizani ndi kukuchenjezani.+

Zikanakhala bwino ngati mukanandimvera, inu Aisiraeli.+

 9 Pakati panu sipadzakhala mulungu wosadziwika.+

Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+

10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,+

Amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.+

Tsegulani pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+

11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga.+

Ndipo Isiraeli sanasonyeze kuti ndi wofunitsitsa kundimvera.+

12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuumitsa mtima wawo.+

Iwo anapitiriza kuyenda mu nzeru zawo.+

13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+

Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+

14 Ndikanagonjetsa adani awo mosavuta,+

Ndipo ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+

15 Koma odana kwambiri ndi Yehova adzabwera kwa iye akunjenjemera ndi mantha,+

Ndipo nthawi yawo idzakhala mpaka kalekale.

16 Ine ndidzadyetsa Aisiraeli tirigu wabwino koposa,+

Ndipo ndidzawapatsa uchi wochokera pathanthwe+ kuti adye ndi kukhuta.”

Nyimbo ya Asafu.

82 Mulungu waima pakati pa msonkhano wake,+

Ndipo akuweruza pakati pa milungu kuti:+

 2 “Kodi mudzaweruza mopanda chilungamo,+

Ndi kukondera anthu oipa kufikira liti?+ [Seʹlah.]

 3 Chitirani chilungamo anthu onyozeka ndi ana amasiye.*+

Chitirani chilungamo anthu osautsika ndi osauka.+

 4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.+

Alanditseni m’manja mwa anthu oipa.”+

 5 Milunguyo siikudziwa kanthu ndipo siikuzindikira.+

Ikuyendayenda mu mdima,+

Ndipo maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+

 6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,+

Ndipo nonsenu ndinu ana a Wam’mwambamwamba.+

 7 Ndithudi, mudzafa mmene anthu onse amafera.+

Ndipo mudzagwa mmene kalonga aliyense amagwera!’”+

 8 Nyamukani inu Mulungu, weruzani dziko lapansi.+

Pakuti inu nokha muyenera kutenga mitundu yonse kukhala yanu.+

Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

83 Inu Mulungu, musakhale chete.+

Musakhale phee osalankhulapo kanthu ndipo musakhale duu osachitapo kanthu, inu Mulungu.+

 2 Taonani! Adani anu akuchita phokoso.+

Anthu odana nanu kwambiri atukula mitu yawo.+

 3 Iwo amakumana mwachinsinsi kuti akambirane zochitira chiwembu anthu anu.+

Ndipo amakonzera chiwembu anthu anu obisika.+

 4 Iwo anena kuti: “Bwerani tiwafafanize kuti asakhalenso mtundu,+

Ndi kuti dzina la Isiraeli lisakumbukikenso.”+

 5 Pakuti ndi mtima wonse, iwo amagawana nzeru,+

Ndipo anapangana pangano lotsutsana ndi inu.+

 6 Amenewa ndi anthu okhala m’mahema a Edomu+ ndi m’mahema a Isimaeli, Amowabu+ ndi Ahagara,+

 7 Agebala, Aamoni,+ Aamaleki,

Afilisiti+ pamodzi ndi anthu a ku Turo.+

 8 Asuri nawonso agwirizana nawo,+

Ndipo amapereka thandizo kwa ana aamuna a Loti.+ [Seʹlah.]

 9 Muwachitire zimene munachitira Midiyani+ ndi Sisera.+

Muwachitirenso zimene munachitira Yabini+ kuchigwa cha Kisoni.+

10 Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+

Anasanduka manyowa a m’nthaka.+

11 Atsogoleri awo muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.+

Ndipo mafumu awo onse muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna.+

12 Iwo anena kuti: “Tiyeni tilande malo amene Mulungu amakhalako kuti akhale athu.”+

13 Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+

Ngati mapesi otengeka ndi mphepo.+

14 Mofanana ndi moto wotentha nkhalango,+

Ndiponso malawi a moto woyaka m’mapiri,+

15 Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+

Ndipo muwasokoneze ndi mphepo yanu yamkuntho.+

16 Achititseni manyazi,+

Kuti anthu afunefune dzina lanu, inu Yehova.+

17 Achite manyazi ndi kusokonezeka nthawi zonse.+

Athedwe nzeru ndi kutheratu,+

18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.

84 Inu Yehova wa makamu,+

Ine ndimakondadi chihema chanu chachikulu!+

 2 Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo.+

Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.+

 3 Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,

Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu.

Namzeze* wadzimangira chisa chake pamenepo,

Ndi kuikamo ana ake!

 4 Odala ndi anthu amene akukhala m’nyumba yanu!+

Iwo akupitirizabe kukutamandani.+ [Seʹlah.]

 5 Odala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+

Amene mtima wawo umalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.+

 6 Poyenda m’chigwa chouma mmene muli zitsamba za baka,*+

Amasandutsa chigwacho kukhala choyenda madzi ochokera pakasupe,

Mlangizi wafunda mawu otamanda.+

 7 Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+

Aliyense wa iwo amaonekera kwa Mulungu mu Ziyoni.+

 8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa,+

Tcherani khutu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]

 9 Inu Mulungu chishango chathu, onani,+

Ndipo yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.+

10 Pakuti kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.+

Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga+

Kuposa kukhala m’mahema a anthu oipa.+

11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+

Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+

Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+

12 Inu Yehova wa makamu, wodala ndi munthu amene amakhulupirira inu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.

85 Inu Yehova, mwasangalala ndi dziko lanu.+

Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+

 2 Mwakhululukira anthu anu zolakwa zawo.+

Mwaphimba machimo awo onse.+ [Seʹlah.]

 3 Mwalamulira mkwiyo wanu wonse,+

Ndipo simunasonyeze kutentha kwa mkwiyo wanu.+

 4 Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale, inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+

Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+

 5 Kodi mupitiriza kutikwiyira mpaka kalekale?+

Kodi mudzasonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?+

 6 Kodi simutitsitsimutsanso+

Kuti anthu anu akondwere chifukwa cha inu?+

 7 Inu Yehova, tisonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha,+

Ndipo tipatseni chipulumutso chanu.+

 8 Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanena,+

Pakuti adzanena za mtendere kwa anthu ake+ ndi kwa okhulupirika ake.

Koma iwo asadzidalire kwambiri ngati kale.+

 9 Ndithudi, chipulumutso chake chili pafupi ndi amene amamuopa,+

Kuti ulemerero ukhale m’dziko lathu.+

10 Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zakumana.+

Chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.+

11 Choonadi chidzaphuka padziko lapansi,+

Ndipo chilungamo chidzayang’ana pansi kuchokera kumwamba.+

12 Yehova nayenso adzapereka zinthu zabwino,+

Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.+

13 Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+

Ndipo chidzapanga njira yotsatira mapazi a Mulungu.+

Pemphero la Davide.

86 Tcherani khutu inu Yehova. Ndiyankheni,+

Pakuti ndasautsika ndipo ndasauka.+

 2 Tetezani moyo wanga pakuti ndine wokhulupirika.+

Inu ndinu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani.+

 3 Ndikomereni mtima inu Yehova,+

Pakuti ndimaitana inu tsiku lonse.+

 4 Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu,+

Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+

 5 Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+

Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.+

 6 Inu Yehova, tcherani khutu ku pemphero langa.+

Ndipo mvetserani mawu a kuchonderera kwanga.+

 7 Pa tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu,+

Ndipo inu mudzandiyankha.+

 8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+

Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+

 9 Mitundu yonse imene munapanga idzabwera kwa inu,+

Ndipo idzagwada pamaso panu, inu Yehova,+

Ndi kulemekeza dzina lanu.+

10 Pakuti inu ndinu wamkulu ndipo mukuchita zinthu zodabwitsa.+

Inu nokha ndinu Mulungu.+

11 Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu.+

Ndidzayenda m’choonadi chanu.+

Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.+

12 Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse,+

Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,

13 Pakuti kukoma mtima kosatha kumene mwandisonyeza ndi kwakukulu,+

Ndipo mwapulumutsa moyo wanga ku Manda, kumalo apansi penipeni.+

14 Inu Mulungu, anthu odzitukumula andiukira.+

Khamu la anthu opondereza anzawo likufunafuna moyo wanga,+

Ndipo sanakuikeni patsogolo pawo.+

15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo,+

Wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+

16 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+

Patsani mtumiki wanu mphamvu,+

Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.+

17 Ikani chizindikiro cha ubwino wanu pa ine,

Kuti anthu odana nane aone zimenezi ndi kuchita manyazi,+

Pakuti inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.+

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.

87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali m’mapiri opatulika.+

 2 Yehova amakonda kwambiri zipata za Ziyoni+

Kusiyana ndi mahema onse a Yakobo.+

 3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ [Seʹlah.]

 4 Ine ndidzatchula Rahabi*+ ndi Babulo+ monga ena mwa amene akundidziwa.

Ponena za Filisitiya,+ Turo ndi Kusi ine ndidzati:

“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+

 5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:

“Aliyense anabadwira mmenemo.”+

Ndipo Wam’mwambamwamba+ adzakhazikitsa mzinda umenewo.+

 6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:+

“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+ [Seʹlah.]

 7 Kudzakhalanso oimba komanso ovina gule wovina mozungulira amene adzati:+

“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”+

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.* Iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa m’banja la Zera.

88 Inu Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,+

Masana ndimafuula kwa inu,+

Usikunso ndimafuula pamaso panu.+

 2 Pemphero langa lidzafika kwa inu.+

Tcherani khutu lanu kuti mumve kuchonderera kwanga.+

 3 Pakuti ine ndakumana ndi masoka ochuluka,+

Ndipo moyo wanga wayandikira ku Manda.+

 4 Anandiika m’gulu la anthu otsikira kudzenje.+

Ndakhala ngati mwamuna wanyonga zake koma wopanda mphamvu.+

 5 Ndakhala womasuka ngati anthu akufa,+

Ngati anthu ophedwa amene agona m’manda,+

Anthu amene simukuwakumbukiranso

Komanso amene sakulandira thandizo kuchokera m’manja mwanu.+

 6 Mwandiika m’dzenje lakuya kwambiri,

M’malo a mdima, m’phompho lalikulu.+

 7 Mkwiyo wanu wagwera pa ine,+

Ndipo mwandisautsa ndi mafunde anu onse amphamvu.+ [Seʹlah.]

 8 Anzanga mwawaika kutali ndi ine.+

Mwandisandutsa chinthu chonyansa kwa iwo.+

Ndatsekerezedwa ndipo sindingathenso kuchoka.+

 9 Diso langa lafooka chifukwa cha kusautsika kwanga.+

Ndaitana inu Yehova tsiku lonse.+

Ndapemphera kwa inu nditakweza manja anga.+

10 Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+

Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+

Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.]

11 Kodi adzalengeza za kukoma mtima kwanu kosatha m’manda?

Kodi adzalengeza za kukhulupirika kwanu m’malo a chiwonongeko?+

12 Kodi zodabwitsa zimene inu mukuchita zidzadziwika mu mdima?+

Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika m’dziko la anthu oiwalika?+

13 Koma ine ndafuulira inu Yehova kupempha thandizo,+

Ndipo m’mawa mapemphero anga amafika kwa inu nthawi zonse.+

14 Inu Yehova, n’chifukwa chiyani mukunditaya?+

N’chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+

15 Kuyambira pa unyamata wanga ndakhala ndikusautsika komanso kutsala pang’ono kufa.+

Ndapirira kwambiri zinthu zoopsa zochokera kwa inu.+

16 Mafunde a mkwiyo wanu woyaka moto andimiza.+

Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandisowetsa chonena.+

17 Zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.+

Zandimiza pa nthawi imodzi.

18 Bwenzi langa ndi mnzanga mwawaika kutali kwambiri.+

Malo a mdima ndiwo anzanga apamtima.+

Masikili.* Salimo la Etani wa m’banja la Zera.+

89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+

Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+

 2 Pakuti ndanena kuti: “Kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhazikika mpaka kalekale.+

Ndipo mwakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba.”+

 3 Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+

Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga,+

 4 ‘Ndidzakhazikitsa mbewu yako mpaka kalekale,+

Ndipo ndidzalimbitsa mpando wako wachifumu+ ku mibadwomibadwo.’” [Seʹlah.]

 5 Inu Yehova, kumwamba kudzatamanda ntchito zanu zodabwitsa.+

Mpingo wa oyera anu udzatamanda kukhulupirika kwanu.

 6 Pakuti ndani kumwamba angayerekezeredwe ndi Yehova?+

Ndani angafanane ndi Yehova pakati pa ana a Mulungu?+

 7 Mulungu ayenera kuopedwa pakati pa gulu lake la oyera.+

Iye ndi wamkulu ndi wochititsa mantha kuposa onse omuzungulira.+

 8 Inu Yehova Mulungu wa makamu,+

Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+

Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+

 9 Nyanja ikadzaza mumailamulira.+

Mafunde ake akamawinduka, inuyo mumawakhalitsa bata.+

10 Mwaphwanya Rahabi*+ ndi kumuchititsa kukhala ngati munthu amene waphedwa.+

Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+

11 Kumwamba ndi kwanu,+ dziko lapansi nalonso ndi lanu.+

Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu.+

12 Munapanga kumpoto ndi kum’mwera.+

Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amafuula mokondwera ndi kutamanda dzina lanu.+

13 Mkono wamphamvu ndi wanu,+

Dzanja lanu ndi lamphamvu,+

Dzanja lanu lamanja ndi lokwezeka.+

14 Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando wanu wachifumu.+

Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zili pamaso panu.+

15 Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala.+

Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova.+

16 Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse.+

Chilungamo chanu chimawakweza,+

17 Pakuti inu ndinu amene mumachititsa mphamvu zawo kukhala zaulemerero.+

Ndipo mwa kukoma mtima kwanu, nyanga* yathu imakwezedwa.+

18 Pakuti chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,+

Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+

19 Pa nthawi imeneyo munalankhula ndi okhulupirika anu mwa masomphenya,+

Ndipo munati:

“Ndapereka thandizo kwa wamphamvu.+

Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+

20 Ndapeza Davide mtumiki wanga,+

Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+

21 Dzanja langa lolimba lidzakhala pa iye.+

Mkono wanga udzamulimbitsa.+

22 Palibe mdani amene adzamupondereza,+

Ndipo palibe mwana aliyense wa anthu oipa amene adzamusautsa.+

23 Ndinaphwanya adani ake zidutswazidutswa ndi kuwachotsa pamaso pake,+

Ndipo odana naye kwambiri ndinapitirizabe kuwamenya.+

24 Kukhulupirika kwanga ndi kukoma mtima kwanga kosatha kuli pa iye,+

Ndipo nyanga yake imakwezedwa m’dzina langa.+

25 Ndinaika ulamuliro wake panyanja,+

Ndipo ndinam’patsa ulamuliro pamitsinje.+

26 Iye amafuula kwa ine kuti, ‘Inu ndinu Atate wanga,+

Mulungu wanga+ ndi Thanthwe la chipulumutso changa.’+

27 Inenso ndidzamuika kukhala mwana woyamba kubadwa,+

Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse a padziko lapansi.+

28 Ndidzamusonyeza kukoma mtima kwanga kosatha mpaka kalekale,+

Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+

29 Ndidzakhazikitsa mbewu yake kwamuyaya,+

Ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo kwa masiku ochuluka ngati masiku a kumwamba.+

30 Ana ake akadzasiya chilamulo changa,+

Ndi kuleka kutsatira zigamulo zanga,+

31 Akadzanyoza mfundo zanga,

Ndi kusasunga malamulo anga,

32 Ine ndidzawaimba mlandu ndi kuwalanga ndi ndodo,+

Ndipo ndidzawalanga ndi zikoti chifukwa cha zolakwa zawo.+

33 Koma kukoma mtima kwanga kosatha sindidzakuchotsa pa iye,+

Ndipo sindidzasiya kukhulupirika kwanga.+

34 Sindidzaphwanya pangano langa,+

Ndipo sindidzasintha mawu otuluka pakamwa panga.+

35 Ndalumbira kamodzi kokha pa kuyera kwanga,+

Davide sindidzamunamiza.+

36 Mbewu yake idzakhala mpaka kalekale,+

Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa pamaso panga.+

37 Udzakhazikika ngati mwezi mpaka kalekale,

Udzakhala ngati mboni yokhulupirika ya m’mlengalengayo.” [Seʹlah.]

38 Koma inu mwataya wodzozedwa wanu moti mukupitiriza kunyansidwa naye,+

Ndipo mwamukwiyira.+

39 Mwakana moipidwa pangano la mtumiki wanu.

Mwanyoza chisoti chake chachifumu mwa kuchiponyera pansi.+

40 Mwagwetsa makola ake onse amiyala.+

Mizinda yake yamipanda yolimba mwaisandutsa mabwinja.+

41 Onse oyenda njira imeneyo afunkha zinthu zake.+

Iye wakhala chinthu chotonzedwa kwa anthu oyandikana naye.+

42 Mwakweza dzanja lamanja la adani ake.+

Mwachititsa adani ake onse kusangalala.+

43 Kuwonjezera apo, mukuonanso lupanga lake ngati mdani,+

Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo.+

44 Mwachititsa kuti kuwala kwake kuthe,+

Mpando wake wachifumu mwauponyera pansi.+

45 Mwafupikitsa masiku a unyamata wake.

Ndipo mwamukulunga ndi manyazi.+ [Seʹlah.]

46 Inu Yehova, kodi mudzadzibisa kufikira liti? Ku nthawi zonse?+

Kodi mkwiyo wanu udzakhalabe ukuyaka ngati moto?+

47 Kumbukirani utali wa moyo wanga.+

Kodi ana onse a anthu munawalenga pachabe?+

48 Kodi pali mwamuna wamphamvu aliyense amene sadzaona imfa?+

Kodi angathe kupulumutsa moyo wake m’dzanja la Manda?+ [Seʹlah.]

49 Kodi zochita zanu zakale zija zosonyeza kukoma mtima kosatha zili kuti, inu Yehova?

Zija zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+

50 Inu Yehova, kumbukirani chitonzo chimene chagwera atumiki anu.+

Kumbukirani kuti ndanyamula pachifuwa panga chitonzo cha mitundu yambiri ya anthu.+

51 Inu Yehova, kumbukirani mmene adani anu alankhulira motonza,+

Mmene atonzera paliponse pamene mapazi a wodzozedwa wanu aponda.+

52 Adalitsike Yehova mpaka kalekale. Ame! Ame!*+

BUKU LACHINAYI

(Masalimo 90 – 106)

Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+

90 Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo+

Ku mibadwomibadwo.+

 2 Mapiri asanabadwe,+

Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+

Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+

 3 Mumabwezera munthu kufumbi,+

Ndipo mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+

 4 Pakuti kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+

Ndiponso zili ngati ulonda umodzi wa usiku.*+

 5 Mwawawonongeratu,+ ndipo amangozimiririka ngati maloto.+

M’mawa amakhala ngati msipu wobiriwira umene watsitsimuka.+

 6 Msipuwo umaphuka ndi kutsitsimuka m’mawa.+

Madzulo umafota kenako umauma.+

 7 Pakuti ife tatha chifukwa cha mkwiyo wanu,+

Ndipo tasokonezeka chifukwa cha kupsa mtima kwanu.+

 8 Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+

Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+

 9 Pakuti masiku athu onse atha chifukwa cha mkwiyo wanu.+

Zaka zathu zafika kumapeto ngati mpweya wotuluka m’mphuno pousa moyo.+

10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70,+

Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80.+

Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.+

Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.+

11 Ndani angadziwe kukula kwa ukali wanu,+

Ndi kukula kwa mkwiyo wanu kumene kumafanana ndi ulemu umene muyenera kulandira?+

12 Tisonyezeni mmene tingawerengere masiku athu+

Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.+

13 Bwererani kwa ife, inu Yehova!+ Kodi mudzatenga nthawi yaitali bwanji musanabwerere kwa ife?+

Timvereni chisoni ife atumiki anu.+

14 M’mawa mutikhutiritse ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+

Kuti tifuule mokondwera ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.+

15 Tichititseni kusangalala kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+

Kwa masiku ofanana ndi zaka zimene taona masoka.+

16 Ntchito zanu zionekere kwa atumiki anu,+

Ndipo ulemerero wanu uonekere pa ana awo.+

17 Ubwino wa Yehova Mulungu wathu ukhale pa ife,+

Ndipo mukhazikitse ntchito ya manja athu.+

Muidalitse ntchito ya manja athu.+

91 Aliyense wokhala m’malo otetezeka+ a Wam’mwambamwamba+

Adzakhala wosungika mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+

 2 Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo,+

Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+

 3 Pakuti iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,+

Ndi ku mliri wobweretsa masautso.+

 4 Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+

Udzathawira pansi pa mapiko ake.+

Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo.

 5 Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+

Ndipo sudzaopanso muvi+ woponyedwa masana,

 6 Sudzaopa mliri umene umayenda mu mdima,+

Kapena chiwonongeko chimene chimachitika dzuwa lili paliwombo.+

 7 Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,

Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.

Koma palibe zoterezi zimene zidzakuchitikira.+

 8 Udzayang’ana ndi maso ako,+

Ndipo udzaona anthu oipa akulandira chilango.+

 9 Popeza wanena kuti: “Yehova ndiye pothawirapo panga,”+

Wapanga Wam’mwambamwamba kukhala malo ako okhalamo.+

10 Palibe tsoka limene lidzakugwera,+

Ndipo ngakhale mliri sudzayandikira hema wako.+

11 Pakuti adzalamula angelo ake za iwe,+

Kuti akuteteze m’njira zako zonse.+

12 Iwo adzakunyamula m’manja mwawo,+

Kuti phazi lako lisawombe mwala uliwonse.+

13 Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,+

Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri ndi chinjoka.+

14 Mulungu wanena kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda,+

Inenso ndidzamupulumutsa.+

Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.+

15 Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+

Ndidzakhala naye m’nthawi ya masautso.+

Ndidzamupulumutsa ndi kumupatsa ulemerero.+

16 Ndidzamukhutiritsa ndi masiku ambiri,+

Ndipo ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la sabata.

92 Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+

Ndi kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+

 2 Ndi bwino kunena za kukoma mtima kwanu kosatha m’mawa,+

Ndi za kukhulupirika kwanu usiku,+

 3 Ndipo ndidzatero pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu.+

Ndidzaimba nyimbo yomveka bwino ndi zeze.+

 4 Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu.

Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.+

 5 Ntchito zanu ndi zazikuludi inu Yehova!+

Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+

 6 Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,+

Ndipo munthu wopusa sangazimvetse.+

 7 Anthu oipa akamaphuka ngati msipu,+

Ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa,

Amatero kuti awonongeke kwamuyaya.+

 8 Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.+

 9 Pakuti taonani adani anu, inu Yehova!+

Adani anu onse adzatha!+

Anthu onse ochita zopweteka anzawo adzamwazikana.+

10 Koma inu mudzakweza nyanga* yanga ngati nyanga ya ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+

Ndidzadzola mafuta abwino.+

11 Diso langa lidzayang’ana adani anga atagonja,+

Makutu anga adzamva za anthu ondiukira, anthu ochita zoipa.

12 Wolungama adzakula ngati mtengo wa kanjedza,+

Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+

13 Anthu obzalidwa m’nyumba ya Yehova,+

M’mabwalo a Mulungu wathu,+ adzakula mosangalala.

14 Zinthu zidzapitiriza kuwayendera bwino ngakhale atachita imvi,+

Adzakhalabe onenepa ndi athanzi,+

15 Kuti alengeze kuti Yehova ndi wolungama.+

Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.+

93 Yehova wakhala mfumu!+

Iye wavala ulemerero.+

Yehova wavala mphamvu ngati chovala, ndipo wamangirira mphamvuzo m’chiuno mwake.+

Dziko lapansi lakhazikika, moti silingagwedezeke.+

 2 Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+

Munakhalako kuyambira kalekale.+

 3 Inu Yehova, mitsinje ikufuula.

Ikufuula ndi mawu amphamvu.+

Mitsinje ikupitiriza kufuula ndi mawu amkokomo.+

 4 Ulemerero wa Yehova ndi waukulu+ kumwamba,

Kuposa mkokomo wa madzi ambiri, kuposanso mafunde amphamvu a m’nyanja.+

 5 Zikumbutso zanu ndi zodalirika zedi.+

Chiyero ndi choyenera nyumba yanu+ mpaka muyaya, inu Yehova.+

94 Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+

Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+

 2 Nyamukani inu Woweruza dziko lapansi.+

Perekani chilango kwa anthu odzikweza.+

 3 Kodi anthu oipa adzakondwera kufikira liti?+

Kodi adzakondwera kufikira liti, inu Yehova?+

 4 Iwo amalankhula zopanda pake, ndipo amalankhula mosasamala.+

Onse ochita zopweteka anzawo amadzitukumula.+

 5 Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+

Ndipo amasautsa cholowa chanu.+

 6 Amapha mkazi wamasiye ndi mlendo wokhala m’dziko lawo,+

Ndipo amaphanso ana amasiye.*+

 7 Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+

Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+

 8 Zindikirani anthu opanda nzeru inu.+

Ndipo opusa inu, mudzakhala liti ozindikira?+

 9 Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve?+

Kapena amene anapanga maso, sangaone?+

10 Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu,+

Amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira, sangathe kudzudzula?+

11 Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+

12 Wodala ndi munthu wamphamvu amene inu Ya mumamudzudzula,+

Komanso amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+

13 Kuti mum’patse mtendere pa nthawi ya masoka,+

Kufikira dzenje la munthu woipa litakumbidwa.+

14 Yehova sadzataya anthu ake,+

Kapena kusiya cholowa chake.+

15 Pakuti zigamulo zidzayambiranso kukhala zachilungamo,+

Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira.

16 Ndani adzanyamuka kuti amenye nkhondo ndi anthu ochita zoipa m’malo mwa ine?+

Ndani adzaima m’malo mwa ine kulimbana ndi anthu ochita zopweteka anzawo?+

17 Yehova akanapanda kundithandiza,+

Ndikanatsikira kuli chete mofulumira.+

18 Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa literereka,”+

Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza.+

19 Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga,+

Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.+

20 Kodi inu mudzagwirizana ndi olamulira ankhanza,+

Pamene akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo?+

21 Iwo amaukira koopsa munthu wolungama,+

Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti ndi woipa. Amachita zimenezi kuti akhetse magazi ake.+

22 Koma Yehova adzakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+

Ndipo Mulungu wanga adzakhala thanthwe langa lothawirako.+

23 Iye adzawabwezera zoipa zawo,+

Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+

Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+

95 Bwerani tifuule kwa Yehova mokondwera!+

Iye amene ndi Thanthwe la chipulumutso chathu, timufuulire mosangalala chifukwa wapambana.+

 2 Tiyeni tionekere pamaso pake ndi chiyamiko.+

Tiyeni tiimbe nyimbo zomutamanda ndi kumufuulira mosangalala chifukwa wapambana.+

 3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,+

Ndiponso ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+

 4 Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali m’manja mwake,+

Mapiri aatali nawonso ndi ake.+

 5 Nyanja imene anapanga ndi yake,+

Iye amenenso anapanga mtunda ndi manja ake.+

 6 Bwerani timuweramire ndi kumupembedza.+

Tiyeni tigwade+ pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga.+

 7 Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.+

Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+

 8 Musaumitse mitima yanu monga mmene makolo anu anachitira pa Meriba,+

Monga mmene anachitira pa Masa m’chipululu,+

 9 Pamene makolo anu anandiyesa.+

Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+

10 Kwa zaka 40, m’badwo umenewo unali kundinyansa,+

Ndipo ndinati:

“Anthu awa mitima yawo imasochera,+

Ndipo sadziwa njira zanga.”+

11 Kunena za anthu amenewa ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti:+

“Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+

96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+

Imbirani Yehova, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+

 2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake.+

Tsiku ndi tsiku lengezani uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+

 3 Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,+

Ndiponso ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+

 4 Pakuti Yehova ndi wamkulu+ ndi woyenera kutamandidwa kwambiri.

Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse.+

 5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+

Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+

 6 Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake.+

Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.+

 7 Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,+

M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+

 8 M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+

Tengani mphatso ndi kulowa m’mabwalo ake.+

 9 Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+

Njenjemerani ndi mantha aakulu* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+

10 Nenani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala mfumu.+

Dziko lapansi nalonso lakhazikika moti silingagwedezeke.+

Iye adzaweruzira mitundu ya anthu milandu yawo mwachilungamo.”+

11 Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale.+

Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo.+

12 Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+

Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera pamaso pa Yehova.+

13 Pakuti iye wabwera.+

Iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+

Adzaweruza dziko mwachilungamo,+

Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

97 Yehova wakhala mfumu!+ Dziko lapansi likondwere,+

Ndipo zilumba zambiri zisangalale.+

 2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+

Chilungamo ndi chiweruzo ndizo malo okhazikika a mpando wake wachifumu.+

 3 Patsogolo pake pakuyaka moto,+

Ndipo ukupsereza adani ake onse omuzungulira.+

 4 Mphezi zake zinawalitsa dziko lapansi.+

Dziko linaona ndipo linachita mantha kwambiri.+

 5 Mapiri anasungunuka ngati phula chifukwa cha Yehova,+

Chifukwa cha Ambuye wa dziko lonse lapansi.+

 6 Kumwamba kwalengeza za chilungamo chake,+

Ndipo mitundu yonse ya anthu yaona ulemerero wake.+

 7 Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+

Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+

Muweramireni, inu milungu yonse.+

 8 Ziyoni anamva ndipo anayamba kusangalala,+

Midzi yozungulira Yuda inayamba kukondwera+

Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+

 9 Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+

Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+

10 Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+

Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+

Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+

11 Kuwala kwaunikira wolungama,+

Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+

12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, anthu olungama inu,+

Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*+

Nyimbo.

98 IMBIRANI Yehova nyimbo yatsopano,+

Pakuti zimene wachita ndi zodabwitsa.+

Dzanja lake lamanja, ndithu mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.+

 2 Yehova wachititsa chipulumutso chake kudziwika.+

Chilungamo chake wachisonyeza ku mitundu ya anthu.+

 3 Iye wakumbukira lonjezo lake losonyeza kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika kwake ku nyumba ya Isiraeli.+

Malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.+

 4 Fuulirani Yehova mosangalala chifukwa wapambana, inu nonse anthu a padziko lapansi.+

Kondwerani, fuulani mosangalala ndi kuimba nyimbo zomutamanda.+

 5 Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda ndi zeze,+

Muimbireni nyimbo ndi zeze ndi kumutamanda ndi nyimbo zokoma.+

 6 Fuulani mwa kuimba malipenga ndi mphalasa.*+

Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova, chifukwa wapambana.

 7 Nyanja ndi zonse zili mmenemo zichite mkokomo,+

Chimodzimodzinso mtunda ndi zonse zokhala kumeneko.+

 8 Mitsinje iwombe m’manja,

Mapiri onse afuule pamodzi mokondwera pamaso pa Yehova.+

 9 Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+

Adzaweruza dziko mwachilungamo,+

Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu molungama.+

99 Yehova wakhala mfumu.+ Mitundu ya anthu inthunthumire.+

Iye wakhala pa akerubi.+ Ndipo dziko lapansi linjenjemere.+

 2 Yehova wasonyeza mu Ziyoni kuti ndi wamkulu,+

Ndipo ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+

 3 Iwo atamande dzina lanu.+

Dzina lanu ndi lalikulu, lochititsa mantha ndi loyera.+

 4 Iye amakonda chilungamo ngati mmene mfumu yamphamvu imachitira.+

Inu mwakhazikitsa kulungama.+

Mwakhazikitsa chiweruzo ndi chilungamo pakati pa ana a Yakobo.+

 5 Kwezani Yehova Mulungu wathu+ ndipo muweramireni pachopondapo mapazi ake.+

Iye ndi woyera.+

 6 Mose ndi Aroni anali pakati pa ansembe ake,+

Samueli anali pakati pa anthu amene anali kuitana pa dzina lake.+

Iwo anali kuitana Yehova, ndipo iye anali kuwayankha.+

 7 Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+

Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+

 8 Inu Yehova Mulungu wathu munawayankha.+

Kwa iwo munasonyeza kuti ndinu Mulungu wokhululuka,+

Ndiponso wopereka chilango chifukwa cha zochita zawo zoipa.+

 9 Kwezani Yehova Mulungu wathu,+

Ndipo weramani paphiri lake loyera.+

Pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.+

Nyimbo yoyamikira.+

100 Fuulirani Yehova mosangalala inu nonse anthu a padziko lapansi chifukwa wapambana.+

 2 Tumikirani Yehova mokondwera.+

Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.+

 3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.+

Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.+

Ndife anthu ake ndi nkhosa zimene akuweta.+

 4 Lowani pazipata zake ndi mawu oyamikira,+

Lowani m’mabwalo ake ndi mawu otamanda.+

Muyamikeni, tamandani dzina lake.+

 5 Pakuti Yehova ndi wabwino.+

Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapo mpaka kalekale,+

Ndipo kukhulupirika kwake kudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

Nyimbo ndi Salimo la Davide.

101 Ndidzaimba za kukoma mtima kwanu kosatha ndi chiweruzo chanu.+

Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.+

 2 Ndidzachita zinthu mwanzeru m’njira yowongoka.+

Kodi inu mudzandithandiza liti?+

Ndidzayendayenda m’nyumba yanga ndi mtima wanga wosagawanika.+

 3 Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.+

Ndimadana ndi zochita za opatuka pa choonadi.+

Sindilola kuti zochita zawozo zindikhudze.+

 4 Aliyense wopotoka maganizo amachoka pamaso panga.+

Sindichita choipa chilichonse.+

 5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+

Ndimamukhalitsa chete.+

Sindingathe kupirira zochita za+

Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+

 6 Maso anga ali pa okhulupirika a padziko lapansi,+

Kuti akhale ndi ine.+

Woyenda m’njira yowongoka,+

Ndi amene adzanditumikira.+

 7 M’nyumba yanga simudzakhala wochita chinyengo.+

Ndipo aliyense wolankhula zachinyengo sadzapitiriza kukhala+

Pamaso panga.+

 8 M’mawa uliwonse ndidzawononga oipa onse a padziko lapansi.+

Ndidzapha ndi kuchotsa mumzinda wa Yehova anthu onse ochita zinthu zopweteka anzawo.+

Pemphero la munthu wosautsika pamene walefuka ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+

102 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+

Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo.+

 2 Musandibisire nkhope yanu pa tsiku limene ndili m’masautso aakulu.+

Tcherani khutu lanu kwa ine.+

Fulumirani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana.+

 3 Pakuti masiku a moyo wanga atha ndi kuzimiririka ngati utsi,+

Ndipo mafupa anga atentha kwambiri ngati ng’anjo.+

 4 Mtima wanga wawauka ngati udzu ndipo wauma,+

Pakuti ndilibe chilakolako chofuna kudya chakudya.+

 5 Chifukwa cha kuusa moyo kwanga,+

Thupi langa langotsala mafupa okhaokha.+

 6 Ndafanana ndi vuwo wam’chipululu.+

Ndakhala ngati nkhwezule yakubwinja.

 7 Ndafika pofooka,

Ndipo ndakhala ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.*+

 8 Tsiku lonse adani anga amanditonza.+

Anthu ondinyoza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.+

 9 Pakuti ndadya phulusa ngati chakudya.+

Ndipo zakumwa zanga ndazisakaniza ndi misozi,+

10 Chifukwa cha kudzudzula kwanu kwamphamvu ndi mkwiyo wanu.+

Inu mwandikweza m’mwamba kuti munditaye.+

11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa,+

Ndipo ndauma ngati udzu.+

12 Koma inu Yehova, mudzakhalapobe kwamuyaya,+

Dzina lanu* lidzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+

13 Inu mudzanyamuka ndi kusonyeza Ziyoni chifundo,+

Pakuti imeneyi ndi nyengo yomukomera mtima,

Chifukwa nthawi yoikidwiratu yakwana.+

14 Atumiki anu akondwera ndi miyala ya mpanda wake,+

Ndipo amakomera mtima fumbi lake.+

15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,+

Ndipo mafumu onse a padziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+

16 Yehova adzamangadi Ziyoni.+

Iye ayenera kuonekera mu ulemerero wake.+

17 Iye adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse,+

Ndipo sadzapeputsa pemphero lawo.+

18 Zimenezi zalembedwera m’badwo wam’tsogolo.+

Ndipo anthu amene adzakhalapo m’tsogolo* adzatamanda Ya.+

19 Iye wayang’ana pansi ali kumalo oyera, okwezeka,+

Yehova wayang’ana dziko lapansi ali kumwambako,+

20 Kuti amve kuusa moyo kwa akaidi,+

Ndi kumasula anthu opita kukaphedwa.+

21 Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe m’Ziyoni,+

Ndi kuti atamandidwe mu Yerusalemu,+

22 Pamene mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa pamodzi,+

Komanso maufumu, kuti atumikire Yehova.+

23 Moyo wanga utafika pachimake, anachepetsa mphamvu zanga,+

Anafupikitsa masiku a moyo wanga.+

24 Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,

Musadule pakati masiku a moyo wanga.+

Mudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

25 Munaika kalekale maziko a dziko lapansi,+

Ndipo kumwamba ndiko ntchito ya manja anu.+

26 Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.+

Ndipo zonsezi zidzatha ngati chovala.+

Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha.+

27 Koma inu simudzasintha, ndipo mudzakhalapo kwamuyaya.+

28 Ana a atumiki anu adzapitiriza kukhala motetezeka pamaso panu.+

Ndipo ana awo adzakhazikika pamaso panu.”+

Salimo la Davide.

103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+

Chilichonse mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.+

 2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,

Ndipo usaiwale zochita zake zonse.+

 3 Tamanda amene akukukhululukira zolakwa zako zonse,+

Iye amene akukuchiritsa matenda ako onse.+

 4 Tamanda amene akuwombola moyo wako kudzenje,+

Amene akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu,+

 5 Amene akukukhutiritsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.+

Mulungu akukuchititsa kukhalabe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+

 6 Yehova akuchitira chilungamo+

Ndi kuperekera zigamulo anthu amene akuchitiridwa zachinyengo.+

 7 Anauza Mose njira zake,+

Ndipo anadziwitsa ana a Isiraeli zochita zake.+

 8 Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo,+

Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+

 9 Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu,+

Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+

10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+

Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+

11 Pakuti monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,+

Kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.+

12 Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+

Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+

13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+

Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+

14 Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira,+

Amakumbukira kuti ndife fumbi.+

15 Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu wobiriwira.+

Iye amaphuka ngati mmene duwa lakutchire limaphukira.+

16 Mphepo ikawomba limafa,+

Ndipo pamalo amene linali sipadziwikanso,+

17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale,+

Kwa anthu amene amamuopa.+

Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+

18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu osunga pangano lake,+

Ndi kwa anthu okumbukira malamulo ake ndi kuwatsatira.+

19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+

Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+

20 Tamandani Yehova, inu angelo+ ake amphamvu, ochita zimene wanena,+

Mwa kumvera malamulo ake.+

21 Tamandani Yehova inu makamu ake onse,+

Inu atumiki ake onse ochita chifuniro chake.+

22 Tamandani Yehova inu ntchito zake zonse,+

M’malo onse amene iye akulamulira.+

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+

104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+

Inu Yehova Mulungu wanga, mwasonyeza kuti ndinu wamkulu koposa.+

Mwadziveka ulemu ndi ulemerero.+

 2 Mwadzifunditsa kuwala ngati chofunda,+

Mwatambasula kumwamba ngati nsalu ya chihema.+

 3 Inu munamanga zipinda za m’mwamba pamadzi pogwiritsa ntchito mitanda,+

Munapanga mitambo kukhala galeta lanu,+

Mumayenda pamapiko a mphepo.+

 4 Inu mumapanga angelo anu kukhala mizimu,+

Ndipo atumiki anu kukhala moto wonyeketsa.+

 5 Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba.+

Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.+

 6 Munalikuta ndi madzi ngati mwalikuta ndi nsalu.+

Madziwo anakwera kupitirira mapiri.+

 7 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anayamba kuthawa.+

Atamva mabingu anu anayamba kuthamanga mopanikizika kwambiri,

 8 Kupita kumalo amene munawakonzera.

Mapiri anakwera,+

Zigwa zinatsika.

 9 Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+

Kuti asamizenso dziko lapansi.+

10 Mwatsegula akasupe m’zigwa,+

Ndipo madziwo akudutsa pakati pa mapiri.

11 Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.+

Nthawi zonse mbidzi+ zimapha ludzu lawo mmenemo.

12 Zolengedwa zouluka m’mlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,+

Ndipo zimalira m’mitengo ya masamba ambiri obiriwira.+

13 Mulungu amathirira mapiri kuchokera m’zipinda zake za m’mwamba.+

Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito yake.+

14 Amameretsa msipu kuti nyama zidye,+

Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+

Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka,+

15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+

Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+

Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+

16 Mitengo ya Yehova imathiriridwa bwino,

Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anabzala.+

17 Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.+

Dokowe nyumba yake ndiyo mitengo ya mlombwa.+

18 M’mapiri aatali+ ndi mmene mumakhala mbuzi zakumapiri.+

Ndipo m’mapanga ndiye mothawiramo mbira.+

19 Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+

Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+

20 Munapanga mdima kuti kukhale usiku.+

Nyama zonse zakutchire zimayendayenda usikuwo.

21 Mkango wamphamvu umabangula pofunafuna nyama,+

Ndiponso popempha chakudya kwa Mulungu.+

22 Dzuwa likayamba kuwala+ zimachoka,

Ndipo zimakagona m’malo awo obisalamo.

23 Munthu amapita ku ntchito zake,+

Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo.+

24 Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+

Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+

Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+

25 M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala,+

Muli zinthu zoyenda zosawerengeka,+

Muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.+

26 Zombo zimayenda mmenemo.+

Ndipo Leviyatani*+ munam’panga kuti azisewera mmenemo.+

27 Zonsezi zimayembekezera inu+

Kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+

28 Zimalandira zimene mwazipatsa.+

Mumatambasula dzanja lanu ndipo zimakhutira ndi zinthu zabwino.+

29 Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+

Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+

Ndipo zimabwerera kufumbi.+

30 Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa.+

Ndipo mumachititsa dziko kukhala latsopano.

31 Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale.+

Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+

32 Amayang’ana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.+

Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+

33 Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse.+

Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+

34 Kulingalira za iye kukhale kosangalatsa.+

Ine ndidzakondwera mwa Yehova.+

35 Ochimwa adzafafanizidwa padziko lapansi.+

Ndipo anthu oipa sadzakhalaponso.+

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Tamandani Ya, anthu inu!*+

105 YAMIKANI Yehova, itanani pa dzina lake,+

Lengezani zochita zake pakati pa mitundu ya anthu.+

 2 Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,+

Sinkhasinkhani ntchito zake zonse zodabwitsa.+

 3 Nyadirani dzina lake loyera.+

Mtima wa anthu ofunafuna Yehova usangalale.+

 4 Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake.+

Funafunani nkhope yake nthawi zonse.+

 5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+

Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+

 6 Inu mbewu ya Abulahamu mtumiki wake,+

Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+

 7 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+

Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+

 8 Wakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+

Wakumbukira lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,+

 9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+

Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki,+

10 Lonjezo limeneli analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,

Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+

11 Pamene anati: “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+

Kuti likhale gawo la cholowa chako.”+

12 Pamene ananena zimenezi, n’kuti iwo ali ochepa.+

N’kuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo m’dzikolo.+

13 Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+

Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+

14 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo,+

Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+

15 Iye anati: “Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,+

Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+

16 Iye anadzetsa njala yaikulu m’dzikomo,+

Ndipo anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati.+

17 Mulungu anatsogoza munthu kuti anthu akewo abwere pambuyo pake,

Anatumiza Yosefe amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+

18 Kumeneko anasautsa mapazi ake ndi matangadza,+

Anam’manga ndi maunyolo.+

19 Mawu a Yehova anamuyenga,+

Kufikira pamene lonjezo la Mulungu linakwaniritsidwa.+

20 Mfumu inalamula kuti amutulutse m’ndende.+

Wolamulira mitundu ya anthu analamula kuti Yosefe amasulidwe.

21 Anamuika kukhala mkulu woyang’anira banja lake,+

Komanso wolamulira chuma chake chonse.+

22 Anamupatsa ulamuliro womanga kalonga aliyense wa mfumu,+

Komanso kuphunzitsa zinthu za nzeru anthu achikulire.+

23 Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo,+

Yakobo anakhala monga mlendo m’dziko la Hamu.+

24 Mulungu anachititsa anthu ake kuberekana,+

Ndipo pang’onopang’ono anawasandutsa anthu amphamvu kuposa adani awo.+

25 Analola adaniwo kusintha mitima yawo ndi kudana ndi anthu ake,+

Anawalola kuchitira atumiki ake zachinyengo.+

26 Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,+

Ndi Aroni amene anamusankha.+

27 Iwowa anasonyeza Aiguputo zizindikiro za Mulungu,+

Ndi zozizwitsa m’dziko la Hamu.+

28 Anatumiza mdima moti kunada.+

Ndipo iwo sanapandukire mawu ake.+

29 Anasandutsa madzi awo kukhala magazi,+

Ndipo anapha nsomba zawo.+

30 M’dziko lawo munadzaza achule,+

Chimodzimodzinso m’zipinda za mafumu awo.

31 Analamula kuti pagwe tizilombo touluka toyamwa magazi,+

Komanso ntchentche zoluma m’madera awo onse.+

32 Anawagwetsera matalala m’malo mwa mvula,+

Anawagwetseranso moto woyaka, walawilawi m’dziko lawo.+

33 Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyu,

Ndipo anakhadzula mitengo m’dziko lawo.+

34 Analamula kuti pagwe dzombe,+

Ndipo panagwa dzombe losawerengeka la mtundu winawake.+

35 Dzombelo linadya zomera zonse m’dziko lawo.+

Linadyanso mbewu zonse za m’munda mwawo.

36 Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko lawo,+

Chiyambi cha mphamvu zawo zonse zobereka.+

37 Ndiyeno anayamba kuwatulutsa atatenga siliva ndi golide.+

Pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.

38 Aiguputo anasangalala pamene Aisiraeli anatuluka m’dzikolo,

Pakuti anali kuwaopa kwambiri.+

39 Mulungu anayala mtambo kuti uziwatchinga,+

Ndipo anawapatsa moto kuti uziwaunikira usiku.+

40 Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,+

Anawadyetsa chakudya chochokera kumwamba.+

41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+

Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+

42 Iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+

43 Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake m’dzikomo anthuwo akusangalala,+

Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera.+

44 Pang’onopang’ono anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+

Ndipo zipatso za ntchito imene mitundu ya anthu inagwira mwakhama, anazitenga kukhala zawo,+

45 Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+

Ndi kusunga malamulo ake.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

106 Tamandani Ya, anthu inu!+

Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 2 Ndani anganene zinthu zamphamvu zimene Yehova wachita,+

Kapena ndani angamutamande mokwanira?+

 3 Odala ndi anthu amene amatsata chilungamo,+

Ndi kuchita zolungama nthawi zonse.+

 4 Ndikumbukireni inu Yehova, ndipo ndisonyezeni kukoma mtima kumene mumasonyeza anthu anu.+

Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,+

 5 Kuti ndione ubwino umene mumapereka kwa osankhidwa anu,+

Kuti ndikondwere pamene mtundu wanu ukukondwera,+

Ndiponso kuti ndinyadire pamodzi ndi cholowa chanu.+

 6 Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+

Tachita zinthu zosayenera, tachita zinthu zoipa.+

 7 Makolo athu ku Iguputo,

Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+

Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+

Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+

 8 Koma Mulungu anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,+

Kuti mphamvu zake zidziwike.+

 9 Choncho anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo pang’onopang’ono nyanjayo inauma.+

Pamenepo anawayendetsa kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akuwayendetsa m’chipululu.+

10 Chotero anawapulumutsa m’manja mwa wodana nawo,+

Ndipo anawawombola m’manja mwa mdani.+

11 Ndiyeno madzi anamiza adani awo,+

Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+

12 Pamenepo anakhulupirira mawu ake,+

Ndipo anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+

13 Koma mofulumira anaiwala ntchito zake,+

Iwo sanayembekezere malangizo ake.+

14 Anasonyeza chikhumbo chawo chadyera m’chipululu,+

Ndipo anayesa Mulungu m’chipululumo.+

15 Mulungu anawapatsa zimene anali kupempha,+

Ndipo anawagwetsera matenda a kaliwondewonde pakati pawo.+

16 Iwo anayamba kuchitira Mose kaduka mumsasa,+

Ndiponso Aroni, woyera wa Yehova.+

17 Pamenepo dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,+

Ndi kufotsera msonkhano wa Abiramu.+

18 Moto unayaka pakati pa msonkhano wawo.+

Malawi amoto ananyeketsa anthu oipawo.+

19 Iwo anapanganso mwana wa ng’ombe ku Horebe,+

Ndipo anaweramira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+

20 Choncho anasinthanitsa ulemerero wanga+

Ndi chifaniziro cha ng’ombe yamphongo yodya udzu.+

21 Iwo anaiwala Mulungu, Mpulumutsi wawo,+

Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+

22 Amene anachita zodabwitsa m’dziko la Hamu,+

Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+

23 Iye anangotsala pang’ono kulamula kuti awawononge,+

Koma Mose wosankhidwa wake,

Anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu,+

Ndi kubweza mkwiyo wake kuti usawawononge.+

24 Iwo anayamba kunyansidwa ndi dziko losiririka,+

Ndipo analibe chikhulupiriro m’mawu ake.+

25 Anapitiriza kung’ung’udza m’mahema awo,+

Moti sanamvere mawu a Yehova.+

26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,+

Kuti adzawapha m’chipululu,+

27 Ndiponso kuti adzachititsa ana awo kuphedwa ndi mitundu ina,+

Ndi kuti adzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+

28 Iwo anayamba kulambira Baala wa ku Peori,+

Ndi kudya nsembe zoperekedwa ku zinthu zakufa.+

29 Pamene anali kukhumudwitsa Mulungu chifukwa cha zochita zawo,+

Pakati pawo panagwa mliri.+

30 Pinihasi ataimirira ndi kuchitapo kanthu,+

Mliriwo unatha.

31 Ndipo Pinihasi anaonedwa kukhala wolungama

Ku mibadwomibadwo mpaka kalekale.+

32 Kuwonjezera pamenepo, iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba,+

Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+

33 Iwo anamukwiyitsa

Ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.+

34 Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+

Mmene Yehova anawauzira.+

35 Iwo anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina,+

Ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo.+

36 Anayamba kutumikira mafano awo,+

Ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.+

37 Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+

Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+

38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+

Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,

Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+

Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+

39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo,+

Zochita zawo zinawalowetsa m’makhalidwe oipa.+

40 Mkwiyo wa Yehova unayamba kuyakira anthu ake,+

Ndipo iye ananyansidwa ndi cholowa chake.+

41 Mobwerezabwereza anali kuwapereka m’manja mwa anthu a mitundu ina,+

Kuti anthu odana nawo awalamulire,+

42 Ndi kuti adani awowo awapondereze,

Komanso kuti awagonjetse.+

43 Nthawi zambiri anali kuwalanditsa,+

Koma iwo anali kumupandukira chifukwa sanali kumumvera,+

Ndipo anali kuwatsitsa chifukwa cha zolakwa zawo.+

44 Mulungu akamva kuchonderera kwawo+

Anali kuona kuvutika kwawo.+

45 Zikatero anali kukumbukira pangano limene anachita ndi iwo,+

Ndipo anali kuwamvera chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwake kosatha.+

46 Ndipo anali kuchititsa kuti anthu onse owagwira ukapolo

Awamvere chisoni.+

47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+

Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+

Kuti titamande dzina lanu loyera,+

Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+

48 Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+

Kuyambira kalekale mpaka kalekale.

Ndipo anthu onse anene kuti, Ame.*+

Tamandani Ya, anthu inu!+

BUKU LACHISANU

(Masalimo 107 – 150)

107 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+

Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 2 Anthu owomboledwa a Yehova anene zimenezi,+

Anthu amene iye wawawombola m’manja mwa mdani,+

 3 Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana,+

Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kolowera dzuwa,+

Kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera.+

 4 Iwo anayendayenda m’chipululu+ mopanda kanthu.+

Sanapeze njira iliyonse yopita kumzinda woti azikhalamo.+

 5 Anali ndi njala komanso ludzu.+

Anafooka kwambiri, kutsala pang’ono kufa.+

 6 Iwo anapitiriza kufuulira Yehova m’masautso awo,+

Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+

 7 Anawayendetsa m’njira yabwino,+

Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+

 8 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

 9 Pakuti iye wapereka madzi kwa anthu aludzu.+

Ndipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+

10 Ena anali kukhala mu mdima, mu mdima wandiweyani,+

Anali akaidi osautsika ndi omangidwa maunyolo,+

11 Chifukwa anachita zinthu mopandukira+ mawu a Mulungu,+

Ndipo ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba.+

12 Choncho mwa kuwadzetsera mavuto, Mulungu anagonjetsa mitima yawo.+

Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.+

13 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo,+

Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+

14 Iye anawatulutsa mu mdima, mu mdima wandiweyani,+

Ndi kudula zingwe zimene anamangidwa nazo.+

15 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

16 Pakuti iye wathyola zitseko zamkuwa,+

Ndipo wadula mipiringidzo yachitsulo.+

17 Anthu amene anali opusa chifukwa cha njira yawo yophwanya malamulo,+

Komanso chifukwa cha zolakwa zawo, pamapeto pake anadzibweretsera masautso.+

18 Moyo wawo unaipidwa ndi chakudya cha mtundu uliwonse,+

Ndipo anafika pazipata za imfa.+

19 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo.+

Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+

20 Iye ananena mawu ndipo anawachiritsa,+

Moti anawapulumutsa kudzenje la manda.+

21 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

22 Iwo apereke nsembe zoyamikira,+

Ndi kulengeza za ntchito zake ndi mfuu yachisangalalo.+

23 Anthu amene amayenda m’zombo panyanja,+

Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+

24 Amenewa ndi amene aona ntchito za Yehova,+

Ndiponso ntchito zake zodabwitsa m’madzi akuya.+

25 Aona mmene amautsira mphepo yamkuntho mwa kungonena mawu,+

Moti nyanjayo imachita mafunde.+

26 Iwo amapita pamwamba,

Kenako amatsika pansi.

Chifukwa cha masoka, mitima yawo imasungunuka.+

27 Amadzandira ndipo amayenda peyupeyu ngati munthu woledzera,+

Ndipo ngakhale nzeru zawo zonse zimasokonezeka.+

28 Iwo amayamba kufuulira Yehova m’masautso awo,+

Ndipo iye amawatulutsa m’mavuto awo.+

29 Iye amachititsa mphepo yamkuntho kukhala bata,+

Moti mafunde a panyanja amadekha.+

30 Iwo amasangalala chifukwa mafundewo atha,

Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.+

31 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

32 Amukweze mumpingo wa anthu,+

Ndipo amutamande m’bwalo la anthu achikulire.+

33 Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,+

Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo opanda madzi.+

34 Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lamchere,+

Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo.

35 Amasandutsa chipululu kukhala dambo la madzi,+

Ndipo dziko lopanda madzi amalisintha kukhala dera la akasupe amadzi.+

36 Kumeneko amakhazikako anthu anjala,+

Kuti amange mzinda woti azikhalamo.+

37 Anthuwo amafesa mbewu ndi kulima minda ya mpesa,+

Kuti akhale ndi zokolola.+

38 Mulungu amawadalitsa moti amachuluka kwambiri,+

Ndipo salola kuti ng’ombe zawo zikhale zochepa.+

39 Koma iwo amakhalanso ochepa ndipo amawerama,+

Chifukwa cha kuponderezedwa, masoka ndi chisoni.+

40 Mulungu akutsanulira mnyozo pa anthu olemekezeka,+

Moti iye akuwachititsa kuyendayenda m’chipululu, mmene mulibe njira.+

41 Koma akuteteza munthu wosauka ku nsautso,+

Ndipo akumuchulukitsa kukhala mabanja ambiri ngati gulu la nkhosa.+

42 Olungama amaona ndi kukondwera.+

Koma anthu onse osalungama amatseka pakamwa.+

43 Wanzeru ndani? Iye aona zimenezi,+

Ndi kuchita chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+

Nyimbo ndi Salimo la Davide.

108 Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani,+

Mtima wanga udzachitanso chimodzimodzi.+

 2 Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+

Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.+

 3 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+

 4 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+

Choonadi chanu chafika kuthambo.+

 5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+

Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+

 6 Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+

Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kundiyankha.+

 7 Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+

“Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu+ ngati gawo la cholowa.+

Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+

 8 Giliyadi+ ndi wanga ndipo Manase+ ndi wanganso.

Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.+

Yuda ndi ndodo yanga ya mtsogoleri wa asilikali.+

 9 Mowabu+ ndi beseni langa losambiramo.+

Ndidzaponyera Edomu+ nsapato zanga.+

Ndidzafuula mosangalala+ chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+

10 Ndani adzandibweretsa kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri?+

Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+

11 Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+

Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+

12 Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+

Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+

13 Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+

Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

109 Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.+

 2 Munthu woipa ndiponso munthu wachinyengo andinenera zoipa ndi pakamwa pawo.+

Iwo anena za ine ndi lilime lonama.+

 3 Andizungulira ndi mawu achidani,+

Ndipo akulimbana nane popanda chifukwa.+

 4 Ndikawasonyeza chikondi amanditsutsa,+

Koma ine ndimapemphera.+

 5 Ndikawachitira zabwino amandibwezera zoipa,+

Ndikawasonyeza chikondi amandibwezera chidani.+

 6 Muikireni woweruza woipa,

Ndipo kudzanja lake lamanja kuime wotsutsana naye.+

 7 Pamene akuweruzidwa amuweruze kuti ndi woipa.

Ndipo pemphero lake likhale tchimo.+

 8 Masiku a moyo wake akhale ochepa.+

Udindo wake monga woyang’anira utengedwe ndi munthu wina.+

 9 Ana ake akhale amasiye,*+

Ndipo mkazi wakenso akhale wamasiye.+

10 Ana ake azingoyendayenda ndithu,+

Ndipo azipemphapempha.

Azichoka m’mabwinja mmene akukhala, n’kupita kukafunafuna chakudya.+

11 Wopereka ngongole yakatapira* atchere msampha pa zonse zimene ali nazo,+

Ndipo anthu achilendo+ afunkhe zinthu zimene wakhetsera thukuta.+

12 Pasapezeke womusonyeza kukoma mtima kosatha,+

Ndipo pasapezeke wokomera mtima ana ake amasiyewo.

13 Mbadwa zake ziphedwe ndi kuchotsedwa m’dziko.+

Dzina lawo lifafanizidwe mu m’badwo wotsatira.+

14 Yehova akumbukire cholakwa cha makolo ake,+

Ndipo tchimo la mayi ake+ lisafafanizidwe.+

15 Tchimo ndi cholakwacho zikhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,+

Ndipo achotse dzina lawo padziko lapansi kuti lisakumbukiridwenso,+

16 Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza kukoma mtima kosatha,+

M’malomwake anapitiriza kuthamangitsa wosautsika ndi wosauka,+

Komanso munthu wa mtima wachisoni kuti amuphe.+

17 Iye anakonda kutemberera ena,+ mwakuti matemberero anabwera kwa iye.+

Koma kudalitsa ena sikunali kumusangalatsa,+

Moti madalitso anali patali ndi iye,+

18 Iye anali kuvala matemberero ngati chovala.+

Matembererowo analowa mwa iye ngati madzi,+

Ndiponso analowa m’mafupa ake ngati mafuta.

19 Kwa iye matembererowo akhale ngati chovala chimene amadziphimba nacho,+

Komanso ngati lamba amene amamanga m’chiuno mwake nthawi zonse.+

20 Amenewa ndi malipiro a Yehova kwa aliyense amene amalimbana nane,+

Ndi kwa amene amakamba zondichitira zinthu zoipa.+

21 Koma inu ndinu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+

Ndikomereni mtima chifukwa cha dzina lanu.+

Ndilanditseni,+ popeza kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwakukulu.

22 Ine ndasautsika ndipo ndasauka,+

Mtima wanga walasika mkati mwanga.+

23 Ine ndiyenera kuchoka mofanana ndi chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa.+

Ndakutumulidwa ngati dzombe.

24 Mawondo anga akugwedezeka chifukwa chosala kudya,+

Ndawonda ndipo ndilibe mafuta alionse odzola.+

25 Kwa iwo ndakhala chinthu choyenera kutonzedwa.+

Akandiona amapukusa mitu yawo.+

26 Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.+

Ndipulumutseni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+

27 Iwo adziwe kuti ili ndi dzanja lanu.+

Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.+

28 Alekeni anditemberere,+

Koma inu mundipatse madalitso.+

Iwo aimirira kuti andiukire koma inu muwachititse manyazi,+

Ndipo ine mtumiki wanu ndisangalale.+

29 Amene akulimbana ndi ine avale manyazi,+

Ndipo adziphimbe ndi manyaziwo ngati akudziphimba ndi malaya akunja odula manja.+

30 Ndidzatamanda kwambiri Yehova ndi pakamwa panga,+

Ndipo ndidzamutamanda pakati pa anthu ambiri.+

31 Pakuti adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,+

Kuti am’pulumutse kwa omuweruza mopanda chilungamo.

Salimo la Davide.

110 Yehova wauza Ambuye wanga kuti:+

“Khala kudzanja langa lamanja+

Kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”+

 2 Yehova adzatambasula ndodo+ yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni+ ndi kunena kuti:

“Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.”+

 3 Anthu ako+ adzadzipereka mofunitsitsa+ pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.+

Wadzikongoletsa ndi ulemerero,+

Ndipo gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.+

 4 Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo). Iye wati:+

“Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+

Monga mwa unsembe wa Melekizedeki!”+

 5 Yehova amene ali kudzanja lako lamanja+

Adzaphwanyaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+

 6 Adzapereka chiweruzo pakati pa anthu a mitundu ina.+

Adzachititsa mitembo ya anthu kupezeka paliponse.+

Adzaphwanyaphwanya mtsogoleri wa dziko la anthu ambiri.+

 7 Panjira, adzamwa madzi a m’chigwa.+

N’chifukwa chake adzatukula kwambiri mutu wake.+

111 Tamandani Ya, anthu inu!+

א [ʼAʹleph]

Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse,+

ב [Behth]

Pakati pa gulu+ la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.+

ג [Giʹmel]

 2 Ntchito za Yehova ndi zazikulu,+

ד [Daʹleth]

Onse amene amasangalala nazo amazisinkhasinkha.+

ה [Heʼ]

 3 Zochita zake+ n’zaulemerero ndi ulemu,+

ו [Waw]

Ndipo chilungamo chake chidzakhalapobe kwamuyaya.+

ז [Zaʹyin]

 4 Iye wakonza zoti ntchito zake zodabwitsa zizikumbukiridwa.+

ח [Chehth]

Yehova ndi wachisomo ndiponso wachifundo.+

ט [Tehth]

 5 Wapereka chakudya kwa anthu omuopa.+

י [Yohdh]

Iye adzakumbukira pangano lake nthawi zonse.+

כ [Kaph]

 6 Wafotokozera anthu ake mphamvu za ntchito zake,+

ל [Laʹmedh]

Mwa kuwapatsa cholowa cha mitundu ina ya anthu.+

מ [Mem]

 7 Ntchito za manja ake zimadziwika ndi choonadi ndiponso chiweruzo.+

נ [Nun]

Malamulo onse amene amapereka ndi odalirika.+

ס [Saʹmekh]

 8 Ndi ochirikizika bwino mpaka muyaya, ndithu mpaka kalekale,+

ע [ʽAʹyin]

Ndipo amawapereka m’choonadi ndiponso molungama.+

פ [Peʼ]

 9 Wawombola anthu ake.+

צ [Tsa·dhehʹ]

Wakhazikitsa pangano lake mpaka kalekale.+

ק [Qohph]

Dzina lake ndi loyera ndi lochititsa mantha.+

ר [Rehsh]

10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.+

ש [Sin]

Onse otsatira malamulo a Mulungu ndi ozindikira.+

ת [Taw]

Iye ayenera kutamandidwa mpaka muyaya.+

112 Tamandani Ya, anthu inu!+

א [ʼAʹleph]

Wodala ndi munthu woopa Yehova,+

ב [Behth]

Munthu amene amasangalala kwambiri+ ndi malamulo ake.+

ג [Giʹmel]

 2 Ana ake adzakhala amphamvu padziko lapansi.+

ד [Daʹleth]

Ndipo m’badwo wa anthu olungama udzadalitsidwa.+

ה [Heʼ]

 3 Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili m’nyumba yake,+

ו [Waw]

Ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+

ז [Zaʹyin]

 4 Waunika mu mdima kuti anthu owongoka mtima aone kuwala.+

ח [Chehth]

Iye ndi wachisomo, wachifundo ndi wolungama.+

ט [Tehth]

 5 Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+

י [Yohdh]

Amachita zinthu mwachilungamo.+

כ [Kaph]

 6 Ndithudi munthu wotero sadzagwedezeka ngakhale pang’ono.+

ל [Laʹmedh]

Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale.+

מ [Mem]

 7 Sadzaopa uthenga woipa.+

נ [Nun]

Mtima wake ndi wokhazikika,+ ndipo umadalira Yehova.+

ס [Saʹmekh]

 8 Mtima wake sungagwedezeke,+ ndipo sadzachita mantha,+

ע [ʽAʹyin]

Pamapeto pake adzayang’ana adani ake atagonjetsedwa.+

פ [Peʼ]

 9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+

צ [Tsa·dhehʹ]

Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+

ק [Qohph]

Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+

ר [Rehsh]

10 Woipa adzaona zimenezi ndipo adzasautsika.+

ש [Shin]

Adzakukuta mano ndi kusungunuka.+

ת [Taw]

Chikhumbo cha anthu oipa chidzatha.+

113 Tamandani Ya, anthu inu!+

Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,+

Tamandani dzina la Yehova.+

 2 Dzina la Yehova lidalitsike,+

Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

 3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,+

Dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.+

 4 Yehova wakwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+

Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+

 5 Ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+

Amene amakhala pamwamba?+

 6 Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+

 7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.+

Amakweza munthu wosauka kumuchotsa padzala,+

 8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,+

Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.+

 9 Akuchititsa mkazi wosabereka kukhala m’nyumba+

Monga mayi wosangalala wa ana aamuna.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

114 Pamene Isiraeli anatuluka mu Iguputo,+

Pamene nyumba ya Yakobo inatuluka pakati pa anthu olankhula zosamveka,+

 2 Yuda anakhala malo ake oyera,+

Ndipo Isiraeli anakhala ufumu wake waukulu.+

 3 Nyanja inaona ndipo inathawa.+

Yorodano anabwerera m’mbuyo.+

 4 Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo,+

Zitunda zinadumphadumpha ngati ana a nkhosa.

 5 Kodi chinavuta n’chiyani nyanja iwe kuti uthawe?+

Kodi iwe Yorodano chinavuta n’chiyani kuti ubwerere m’mbuyo?+

 6 Nanga inu mapiri, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati nkhosa zamphongo?+

Inunso zitunda, chinavuta n’chiyani kuti mudumphedumphe ngati ana a nkhosa?+

 7 Chifukwa cha Ambuye, chita mantha aakulu dziko lapansi iwe,+

Chita mantha aakulu chifukwa cha Mulungu wa Yakobo,

 8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,+

Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.+

115 Ife sitikuyenerera kalikonse, inu Yehova, ife sitikuyenerera kalikonse,+

Koma dzina lanu ndi loyenera kulemekezedwa+

Malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha, malinganso ndi choonadi chanu.+

 2 Musalole kuti mitundu izinena kuti:+

“Mulungu wawo ali kuti tsopano?”+

 3 Koma Mulungu wathu ali kumwamba.+

Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.+

 4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+

Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+

 5 Pakamwa ali napo koma salankhula,+

Maso ali nawo koma saona.+

 6 Makutu ali nawo koma satha kumva.+

Mphuno ali nayo koma sanunkhiza.+

 7 Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu.+

Mapazi ali nawo koma sayenda.+

Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+

 8 Amene amawapanga adzafanana nawo.+

Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+

 9 Iwe Isiraeli, khulupirira Yehova.+

Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.+

10 Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova.+

Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+

11 Inu oopa Yehova, khulupirirani Yehova.+

Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.+

12 Yehova watikumbukira, ndipo adzapereka madalitso,+

Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli,+

Adzadalitsa nyumba ya Aroni.+

13 Yehova adzadalitsa anthu omuopa,+

Adzadalitsa onsewo osasiyapo aliyense.+

14 Yehova adzakuchulukitsani,+

Inu ndi ana anu.+

15 Inu ndinu amene mwadalitsidwa ndi Yehova,+

Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+

16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+

Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+

17 Akufa satamanda Ya,+

Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+

18 Koma ife tidzatamanda Ya+

Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

116 Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva+

Mawu anga ndi madandaulo anga.+

 2 Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+

Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+

 3 Zingwe za imfa zinandizungulira+

Ndipo ndinasautsika ngati kuti ndili m’Manda.+

Ndinapitiriza kusautsika ndi kukhala wachisoni,+

 4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+

“Inu Yehova, pulumutsani moyo wanga!”+

 5 Yehova ndi wachisomo ndi wolungama.+

Mulungu wathu amasonyeza chifundo.+

 6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+

Ndinali wosautsika koma iye anandipulumutsa.+

 7 Iwe moyo wanga, bwerera kumalo ako ampumulo,+

Pakuti Yehova wakuchitira zinthu zabwino.+

 8 Pakuti inu mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,+

Mwateteza maso anga kuti asakhetse misozi ndiponso phazi langa kuti lisapunthwe.+

 9 Ndidzayenda+ pamaso pa Yehova m’dziko la anthu amoyo.+

10 Ndinali ndi chikhulupiriro,+ n’chifukwa chake ndinalankhula.+

Ndinali kusautsika kwambiri.

11 Pamene ndinapanikizika ndinati:+

“Munthu aliyense ndi wabodza.”+

12 Yehova ndidzamubwezera chiyani+

Pa zabwino zonse zimene wandichitira?+

13 Ndidzamwa za m’kapu yachipulumutso chachikulu,+

Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+

14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+

Pamaso pa anthu ake onse.

15 M’maso mwa Yehova

Imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.+

16 Inu Yehova,+

Inetu ndine mtumiki wanu.+

Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.+

Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+

17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+

Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+

18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+

Ndidzawakwaniritsa pamaso pa anthu ake onse,+

19 M’mabwalo a nyumba ya Yehova,+

Pakati pa iwe Yerusalemu.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

117 Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu.+

Mulemekezeni, inu mafuko onse.+

 2 Pakuti kukoma mtima kosatha kumene watisonyeza ndi kwakukulu.+

Ndipo choonadi+ cha Yehova chidzakhalapobe mpaka kalekale.

Tamandani Ya, anthu inu!+

118 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+

Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 2 Tsopano Isiraeli anene kuti:

“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+

 3 A nyumba ya Aroni anene kuti:+

“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+

 4 Oopa Yehova anene kuti:+

“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+

 5 M’masautso anga ndinaitana Ya.+

Ya anandiyankha ndi kundiika pamalo otakasuka.+

 6 Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+

Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+

 7 Yehova ali kumbali yanga pamodzi ndi anthu amene akundithandiza,+

Ndipo ine ndidzayang’ana anthu odana nane atagonja.+

 8 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+

Kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.+

 9 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+

Kusiyana ndi kudalira anthu olemekezeka.+

10 Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,+

Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+

11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.+

Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.

12 Inandizungulira ngati njuchi,+

Koma inazima ngati moto wa zitsamba zaminga.+

Ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+

13 Munandikankha kwambiri kuti ndigwe,+

Koma Yehova anandithandiza.+

14 Ya ndiye malo anga obisalapo ndi mphamvu zanga,+

Iye amandipulumutsa.+

15 M’mahema+ a olungama+

Mumamveka mfuu yachisangalalo ndipo muli chipulumutso.+

Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+

16 Dzanja lamanja la Yehova likudzikweza pamwamba.+

Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+

17 Sindidzafa, koma ndidzakhalabe ndi moyo,+

Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+

18 Ya anandilanga mwamphamvu,+

Koma sanandipereke ku imfa.+

19 Nditsegulireni zipata zachilungamo,+ anthu inu.

Ndidzalowamo ndipo ndidzatamanda Ya.+

20 Ichi ndi chipata cha Yehova.+

Olungama adzalowamo.+

21 Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+

Ndi kundipulumutsa.+

22 Mwala umene omanga nyumba anaukana+

Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+

23 Umenewu wachokera kwa Yehova,+

Ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu.+

24 Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.+

Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.+

25 Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni.+

Haa! Inu Yehova, chonde tithandizeni kuti zinthu zitiyendere bwino.+

26 Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.+

Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.+

27 Yehova ndiye Mulungu,+

Ndipo amatipatsa kuwala.+

Kongoletsani gulu la anthu amene ali pachikondwerero+ ndi nthambi za mitengo,+ anthu inu.

Likongoletseni mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakutamandani.+

Ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.+

29 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+

Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

א [ʼAʹleph]

119 Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo,+

Anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.+

 2 Odala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+

Amene amayesetsa kumufunafuna ndi mtima wonse.+

 3 Ndithu, iwo sachita chinthu chosalungama.+

Amayenda m’njira zake.+

 4 Inu mwatilamula kuti tisunge+

Malamulo anu mosamala.+

 5 Haa! Ndikanakonda kuti ndiyende mowongoka+

Kuti ndisunge malangizo anu,+

 6 Pamenepo sindikanachita manyazi,+

Pamene ndikulabadira malamulo anu onse.+

 7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,+

Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.+

 8 Ndikupitiriza kusunga malangizo anu,+

Choncho musandisiyiretu.+

ב [Behth]

 9 Kodi wachinyamata+ angakhale bwanji woyera pa moyo wake?

Mwa kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu anu.+

 10 Ndayesetsa kukufunafunani ndi mtima wanga wonse.+

Musandichititse kusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+

 11 Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga,+

Kuti ndisakuchimwireni.+

 12 Ndinu wodala inu Yehova.

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

 13 Ndi milomo yanga ndalengeza+

Zigamulo zonse zotuluka pakamwa panu.+

 14 Ndimakondwera kuyenda m’njira ya zikumbutso zanu,+

Ngati mmene anthu amachitira akapeza chuma chilichonse chamtengo wapatali.+

 15 Ndidzasinkhasinkha malamulo anu,+

Ndipo ndidzalabadira njira zanu.+

 16 Ndidzakonda malamulo anu.+

Ndipo sindidzaiwala mawu anu.+

ג [Giʹmel]

 17 Ndichitireni zabwino, ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo,+

Ndi kuti ndisunge mawu anu.+

 18 Tsegulani maso anga kuti ndione+

Zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.+

 19 Ine ndine mlendo m’dziko ili.+

Musandibisire malamulo anu.+

 20 Moyo wanga wasautsika chifukwa cholakalaka+

Zigamulo zanu nthawi zonse.+

 21 Mwadzudzula odzikuza otembereredwa,+

Amene akusochera ndi kuchoka pa malamulo anu.+

 22 Mugubuduze ndi kuchotsa chitonzo ndi kunyozedwa kwanga,+

Pakuti ndasunga zikumbutso zanu.+

 23 Akalonga asonkhana pamodzi kuti akambirane zondiukira.+

Koma ine mtumiki wanu, ndimasinkhasinkha malangizo anu.+

 24 Ndimakonda zikumbutso zanu,+

Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo.+

ד [Daʹleth]

 25 Moyo wanga wamamatira kufumbi.+

Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+

 26 Ndakuuzani za njira zanga kuti mundiyankhe.+

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

 27 Ndithandizeni kumvetsa njira zofotokozedwa m’malamulo anu,+

Kuti ndisinkhesinkhe ntchito zanu zodabwitsa.+

 28 Ine ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.+

Ndilimbitseni ndi mawu anu.+

 29 Ndichotsereni njira yolakwika,+

Ndikomereni mtima mwa kundipatsa chilamulo chanu.+

 30 Ine ndasankha kuyenda mokhulupirika.+

Zigamulo zanu ndimaziona kukhala zoyenera.+

 31 Ndamamatira zikumbutso zanu.+

Inu Yehova, musandichititse manyazi.+

 32 Ndidzamvera malamulo anu,+

Chifukwa mwandichititsa kuwamvetsa bwino.+

ה [Heʼ]

 33 Ndilangizeni inu Yehova, kuti ndiyende motsatira malangizo anu,+

Kuti nditsatire malangizo anu moyo wanga wonse.+

 34 Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu,+

Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.+

 35 Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu,+

Pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.+

 36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uziganizira zikumbutso zanu,+

Osati kupeza phindu.*+

 37 Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.+

Ndiyendetseni m’njira yanu kuti ndikhalebe wamoyo.+

 38 Kwaniritsani mawu anu pa mtumiki wanu,+

Mawu amene amachititsa mtumiki wanu kukuopani.+

 39 Ndichotsereni chitonzo chimene ndikuchiopa,+

Pakuti zigamulo zanu ndi zabwino.+

 40 Taonani! Ine ndikulakalaka malamulo anu.+

Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.+

ו [Waw]

 41 Monga mwa mawu anu, inu Yehova, ndipatseni chipulumutso chanu.+

Ndipatseni zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha,+

 42 Kuti ndipeze choyankha kwa wonditonza,+

Pakuti ine ndakhulupirira mawu anu.+

 43 Musachotse mawu a choonadi pakamwa panga,+

Pakuti ndayembekezera chigamulo chanu.+

 44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,+

Mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

 45 Ndidzayenda uku ndi uku m’malo otakasuka,+

Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+

 46 Komanso ndidzanena za zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,+

Ndipo sindidzachita manyazi.+

 47 Ndidzakondwera ndi malamulo anu+

Amene ndimawakonda.+

 48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+

Ndipo ndidzasinkhasinkha malangizo anu.+

ז [Zaʹyin]

 49 Kumbukirani mawu amene munandiuza ine mtumiki wanu,+

Mawu amene ndikuwayembekezera malinga ndi lonjezo lanu.+

 50 Chimenechi ndi chilimbikitso changa mu nsautso yanga,+

Pakuti mawu anu andisungabe wamoyo.+

 51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.+

Koma ine sindinapatuke pa chilamulo chanu.+

 52 Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale inu Yehova,+

Ndipo zimandilimbikitsa.+

 53 Mkwiyo ukuyaka mumtima mwanga chifukwa cha oipa,+

Amene akusiya chilamulo chanu.+

 54 Kwa ine, malangizo anu akhala ngati nyimbo zokutamandani,+

M’nyumba zimene ndimakhala m’mayiko achilendo.+

 55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+

Kuti ndisunge chilamulo chanu.+

 56 Ndi zimenetu zandichitikira ine,

Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.+

ח [Chehth]

 57 Yehova, inu ndiye cholowa changa.+

Ndalonjeza kusunga mawu anu.+

 58 Ndayesetsa ndi mtima wanga wonse kuti mundiyanje.*+

Ndikomereni mtima monga mwa mawu anu.+

 59 Ndaganizira mozama za njira zanga,+

Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+

 60 Ndinafulumira ndipo sindinazengereze+

Kusunga malamulo anu.+

 61 Zingwe za oipa zinandikulunga,+

Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+

 62 Pakati pa usiku ndimadzuka kuti ndikuyamikeni+

Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+

 63 Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani,+

Ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.+

 64 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kwadzaza dziko lonse lapansi.+

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

ט [Tehth]

 65 Inu Yehova, mwandichitiradi zabwino ine mtumiki wanu,+

Monga mwa mawu anu.+

 66 Ndiphunzitseni kuchita zabwino,+ kulingalira bwino+ ndi kudziwa zinthu,+

Pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.+

 67 Ndisanagwe m’masautso ndinali kuchimwa mosadziwa,+

Koma tsopano ndimasunga mawu anu.+

 68 Inu ndinu wabwino ndipo mukuchita zabwino.+

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

 69 Anthu odzikuza andinenera mabodza ambiri,+

Koma ine ndidzasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.+

 70 Mitima yawo yauma ngati mafuta oundana,+

Koma ine ndimakonda chilamulo chanu.+

 71 Zili bwino kuti ndasautsika,+

Kuti ndiphunzire malamulo anu.+

 72 Chilamulo+ chotuluka pakamwa panu n’chabwino kwa ine,+

N’chabwino kwambiri kuposa ndalama masauzande zagolide ndi zasiliva.+

י [Yohdh]

 73 Manja anu anandipanga, ndipo anandiumba.+

Ndithandizeni kukhala wozindikira, kuti ndiphunzire malamulo anu.+

 74 Oopa inu ndi amene amasangalala akandiona,+

Chifukwa ndayembekezera mawu anu.+

 75 Inu Yehova, ndikudziwa bwino kuti zigamulo zanu ndi zolungama,+

Ndiponso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+

 76 Kukoma mtima kwanu kosatha kundilimbikitse,+

Monga mwa mawu anu kwa ine mtumiki wanu.+

 77 Ndisonyezeni chifundo chanu kuti ndikhalebe ndi moyo,+

Pakuti ndimakonda chilamulo chanu.+

 78 Odzikuza achite manyazi, chifukwa andisocheretsa popanda chifukwa,+

Koma ine ndimasinkhasinkha malamulo anu.+

 79 Anthu okuopani abwerere kwa ine,+

Chimodzimodzinso odziwa zikumbutso zanu.+

 80 Mtima wanga usunge malangizo anu mosalakwitsa kanthu,+

Kuti ndisachite manyazi.+

כ [Kaph]

 81 Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu,+

Pakuti ndayembekezera mawu anu.+

 82 Maso anga alefuka chifukwa cholakalaka mawu anu,+

Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+

 83 Ndakhala ngati thumba lachikopa+ mu utsi,

Koma sindinaiwale malangizo anu.+

 84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira kufikira liti?+

Kodi anthu ondizunza mudzawaweruza liti?+

 85 Anthu amene sachita zinthu mogwirizana ndi chilamulo chanu,+

Anthu odzikuza akumba mbuna kuti andigwire.+

 86 Malamulo anu onse ndi odalirika.+

Odzikuza andizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+

 87 Iwo anangotsala pang’ono kundifafaniza padziko lapansi,+

Koma ine sindinasiye malamulo anu.+

 88 Ndisungeni wamoyo monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+

Kuti ndisunge zikumbutso zotuluka pakamwa panu.+

ל [Laʹmedh]

 89 Inu Yehova, mawu anu anakhazikika kumwamba,+

Mpaka kalekale.+

 90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwomibadwo.+

Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lisagwedezeke.+

 91 Chilengedwe chonse chakhalapobe kufikira lero chifukwa cha zigamulo zanu,+

Pakuti chilengedwe chonse chimakutumikirani.+

 92 Ndikanapanda kukonda chilamulo chanu,+

Ndikanatheratu m’masautso anga.+

 93 Sindidzaiwala malamulo anu mpaka kalekale,+

Chifukwa mwandisungabe wamoyo kudzera m’malamulo amenewo.+

 94 Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,+

Chifukwa ndaphunzira malamulo anu ndi kuwasunga.+

 95 Oipa amandiyembekezera kuti andiwononge,+

Koma ine ndimamvetsera zikumbutso zanu.+

 96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire.+

Koma malamulo anu amakhudza mbali zonse.

מ [Mem]

 97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+

Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.+

 98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+

Chifukwa ndi anga mpaka kalekale.+

 99 Ndakhala wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga,+

Chifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.+

100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,+

Chifukwa ndimasunga malamulo anu.+

101 Ndaletsa mapazi anga kuyenda m’njira iliyonse yoipa.+

Ndachita izi kuti ndisunge mawu anu.+

102 Sindinapatuke pa zigamulo zanu,+

Pakuti inu mwandilangiza.+

103 Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga,

Kuposa mmene uchi umakomera!+

104 Chifukwa cha malamulo anu ndimachita zinthu mozindikira.+

N’chifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+

נ [Nun]

105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,+

Ndi kuwala kounikira njira yanga.+

106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,+

Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.+

107 Ndasautsika kwambiri.+

Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo monga mwa mawu anu.+

108 Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga,+

Ndipo ndiphunzitseni zigamulo zanu.+

109 Moyo wanga uli pangozi nthawi zonse,*+

Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+

110 Oipa anditchera msampha,+

Koma ine sindinasochere ndi kuchoka pa malamulo anu.+

111 Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale,+

Pakuti zimakondweretsa mtima wanga.+

112 Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu,+

Mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.+

ס [Saʹmekh]

113 Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,+

Koma ndimakonda chilamulo chanu.+

114 Inu ndinu malo anga obisalamo ndi chishango changa,+

Pakuti ndayembekezera mawu anu.+

115 Ndichokereni anthu ochita zoipa inu,+

Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.+

116 Inu Mulungu, ndithandizeni monga mwa mawu anu kuti ndikhalebe ndi moyo,+

Ndipo musandichititse manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.+

117 Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe,+

Ndipo ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse.+

118 Onse osochera ndi kuchoka pa malangizo anu mwawataya kutali,+

Pakuti ndi achinyengo komanso onama.+

119 Anthu onse oipa mwawachotsa padziko lapansi ngati zonyansa.*+

N’chifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.+

120 Chifukwa choopa inu, thupi langa linagwidwa nthumanzi,+

Ndipo chifukwa cha zigamulo zanu, ndinachita mantha.+

ע [ʽAʹyin]

121 Ndapereka ziweruzo zolungama ndipo ndachita zinthu mwachilungamo.+

Musandipereke kwa anthu ondichitira chinyengo.+

122 Khalani ngati chikole kwa ine mtumiki wanu kuti mudzandichitira zabwino.+

Anthu odzikuza asandichitire chinyengo.+

123 Maso anga afooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu+

Ndi mawu anu olungama.+

124 Ndichitireni zabwino ine mtumiki wanu monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha,+

Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+

125 Ine ndine mtumiki wanu.+ Ndithandizeni kukhala wozindikira,+

Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.+

126 Ino ndi nthawi yakuti inu Yehova muchitepo kanthu,+

Chifukwa anthu odzikuzawo aphwanya chilamulo chanu.+

127 N’chifukwa chake ine ndimakonda malamulo anu+

Kuposa golide, golide woyenga bwino.+

128 Choncho ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama.+

Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+

פ [Peʼ]

129 Zikumbutso zanu n’zodabwitsa.+

N’chifukwa chake ine ndimazisunga.+

130 Kuululidwa kwa mawu anu kumapereka kuwala,+

Kumathandiza anthu osadziwa zambiri kukhala ozindikira.+

131 Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndipume mofulumira,+

Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+

132 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima,+

Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu okonda dzina lanu.+

133 Mwapondetsa mwamphamvu mapazi anga pa mawu anu,+

Ndipo musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+

134 Ndiwomboleni kwa munthu aliyense wondichitira zachinyengo,+

Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.+

135 Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu,+

Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+

136 Misozi yatsika m’maso mwanga ngati mitsinje ya madzi,+

Chifukwa chakuti iwo sanasunge chilamulo chanu.+

צ [Tsa·dhehʹ]

137 Ndinu wolungama inu Yehova,+

Ndipo zigamulo zanu ndi zowongoka.+

138 M’chilungamo chanu ndiponso kukhulupirika kwanu kosaneneka+

Mwatilamula kuti tisunge zikumbutso zanu.+

139 Changu changa chandidya,+

Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.+

140 Mawu anu ndi oyengeka kwambiri,+

Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+

141 Kwa ena ndine wopanda pake ndi wonyozeka.+

Koma sindinaiwale malamulo anu.+

142 Chilungamo chanu ndi chilungamo mpaka kalekale,+

Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi.+

143 Zowawa ndi zovuta zinandigwera.+

Koma ndinakonda malamulo anu.+

144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.+

Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti ndikhalebe ndi moyo.+

ק [Qohph]

145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse.+ Ndiyankheni inu Yehova.+

Ndidzasunga malangizo anu.+

146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!+

Ndidzasunga zikumbutso zanu.+

147 Ndadzuka m’mawa kuli mbuu,+ kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+

Pakuti ndayembekezera mawu anu.+

148 Ndimadzuka pa ulonda wa usiku,+

Kuti ndisinkhesinkhe mawu anu.+

149 Imvani mawu anga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+

150 Okonda kuchita khalidwe lotayirira+ abwera pafupi ndi ine.

Iwo atalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.+

151 Inu Yehova muli pafupi,+

Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi.+

152 Zina mwa zikumbutso zanu ndinazidziwa kale kwambiri,+

Pakuti munazikhazikitsa kalekale.+

ר [Rehsh]

153 Onani kusautsika kwanga ndipo ndipulumutseni,+

Pakuti sindinaiwale chilamulo chanu.+

154 Ndiyankhireni mlandu wanga ndi kundipulumutsa.+

Ndisungeni wamoyo mogwirizana ndi mawu anu.+

155 Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa,+

Pakuti sanaphunzire malamulo anu ndi kuwasunga.+

156 Chifundo chanu n’chachikulu, inu Yehova.+

Ndisungenibe wamoyo mogwirizana ndi zigamulo zanu.+

157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+

Koma ine sindinapatuke pa zikumbutso zanu.+

158 Ndaona anthu ochita zinthu mwachinyengo,+

Ndipo amandinyansa chifukwa sasunga mawu anu.+

159 Onani kuti ndimakonda malamulo anu.+

Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+

Ndipo chigamulo chanu chilichonse cholungama chidzakhalapo mpaka kalekale.+

ש [Sin] kapena kuti [Shin]

161 Akalonga andizunza popanda chifukwa,+

Koma mtima wanga umaopa mawu anu.+

162 Ndikukondwera chifukwa cha mawu anu,+

Monga mmene munthu amachitira akapeza zofunkha zambiri.+

163 Ndimadana ndi chinyengo+ ndipo chimandinyansa,+

Koma ndimakonda chilamulo chanu.+

164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,+

Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.+

165 Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka,+

Ndipo palibe chowakhumudwitsa.+

166 Ndayembekezera chipulumutso chanu, inu Yehova,+

Ndipo ndatsatira malamulo anu.+

167 Ndasunga zikumbutso zanu,+

Ndipo ndimazikonda kwambiri.+

168 Ndasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,+

Pakuti njira zanga zonse zili pamaso panu.+

ת [Taw]

169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kochonderera.+

Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, monga mwa mawu anu.+

170 Pempho langa lakuti mundichitire chifundo lifike kwa inu.+

Ndipulumutseni monga mwa mawu anu.+

171 Milomo yanga itulutse mawu okutamandani,+

Pakuti mwandiphunzitsa malamulo anu.+

172 Lilime langa liimbe za mawu anu,+

Pakuti malamulo anu onse ndi olungama.+

173 Dzanja lanu lindithandize,+

Chifukwa ndasankha malamulo anu.+

174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,+

Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+

175 Ndisungenibe wamoyo kuti ndikutamandeni,+

Zigamulo zanu zindithandize.+

176 Ndayendayenda ngati nkhosa yosochera.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,+

Pakuti sindinaiwale malamulo anu.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

120 Ndinafuulira Yehova m’masautso anga,+

Ndipo iye anandiyankha.+

 2 Inu Yehova, ndilanditseni ku milomo yonama,+

Ndi ku lilime lachinyengo.+

 3 Kodi iwe lilime lachinyengo,+

Munthu adzakupatsa chiyani ndipo adzawonjezera chiyani pa iwe?

 4 Adzakupatsa mivi yakuthwa ya munthu wamphamvu,+

Pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa m’chipululu.+

 5 Tsoka kwa ine! Chifukwa ndakhala mlendo m’dziko la Meseke.+

Ndakhala muhema pakati pa mahema a Kedara.+

 6 Ndakhala mumsasa nthawi yaitali+

Pamodzi ndi anthu odana ndi mtendere.+

 7 Ndimalimbikitsa mtendere,+ koma ndikalankhula,

Iwo amafuna nkhondo.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

121 Ndakweza maso anga kuyang’ana kumapiri.+

Kodi thandizo langa lichokera kuti?+

 2 Thandizo langa lichokera kwa Yehova,+

Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+

 3 Iye sangalole kuti phazi lako lipunthwe.+

Amene amakuyang’anira sangawodzere.+

 4 Taonani! Amene akuyang’anira Isiraeli,+

Sangawodzere kapena kugona.+

 5 Yehova akukuyang’anira.+

Yehova ndiye mthunzi wako+ kudzanja lako lamanja.+

 6 Masana dzuwa silidzakupweteka,+

Kapenanso mwezi usiku.+

 7 Yehova adzakuteteza ku masoka onse.+

Iye adzateteza moyo wako.+

 8 Yehova adzakuteteza pa zochita zako zonse,+

Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.

122 Ndinakondwera pamene anandiuza kuti:+

“Tiyeni tipite+ kunyumba ya Yehova.”+

 2 Mapazi athu anaima+

Pazipata zako iwe Yerusalemu.+

 3 Mzinda wa Yerusalemu unamangidwa+

Ngati chinthu chimodzi chogwirizana,+

 4 Mafuko amapita kumeneko,+

Mafuko a Ya,+

Amapita kumeneko kukatamanda dzina la Yehova+

Mogwirizana ndi lamulo loperekedwa kwa Isiraeli.+

 5 Kumeneko n’kumene kumakhala mipando yachiweruzo,+

Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+

 6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu, anthu inu.+

Amene amakukonda, mzinda iwe, sadzakhala ndi nkhawa iliyonse.+

 7 M’malo ako otchingidwa ndi khoma lolimba mupitirizebe kukhala mtendere,+

Anthu okhala munsanja zako apitirizebe kukhala opanda nkhawa iliyonse.+

 8 Tsopano ndikulankhula m’malo mwa abale anga ndi anzanga kuti:+

“Mtendere ukhale nawe.”+

 9 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+

Ndidzapitiriza kukupempherera kuti zinthu zikuyendere bwino.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

123 Ndakweza maso anga kuyang’ana inu,+

Kuyang’ana inu amene mukukhala kumwamba.+

 2 Taonani! Monga mmene maso a atumiki amayang’anira dzanja la mbuye wawo,+

Mmene maso a kapolo wamkazi amayang’anira dzanja la mbuye wake wamkazi,+

Momwemonso, maso athu adzayang’ana kwa Yehova Mulungu wathu,+

Kufikira atatikomera mtima.+

 3 Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,+

Pakuti tanyozeka kwambiri.+

 4 Moyo wathu wasautsika kwambiri chifukwa cha kunyoza kwa anthu amene akukhala mosatekeseka,+

Ndiponso chifukwa cha kunyoza kwa anthu odzikuza.+

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.

124 “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,”+

Isiraeli anene kuti,+

 2 “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,+

Pamene anthu anatiukira,+

 3 Akanatimeza amoyo,+

Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+

 4 Pamenepo madzi akanatikokolola,+

Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+

 5 Madzi amphamvu

Akanatimiza.+

 6 Yehova atamandike, chifukwa sanatipereke kwa iwo+

Kuti atikhadzule ngati nyama.+

 7 Moyo wathu uli ngati mbalame imene yathawa+

Pamsampha wa munthu wogwiritsa ntchito nyambo.+

Msamphawo wathyoka,+

Ndipo ife tapulumuka.+

 8 Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova,+

Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.”+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

125 Okhulupirira Yehova+

Ali ngati phiri la Ziyoni,+ limene silingagwedezeke, koma lidzakhalapo mpaka kalekale.+

 2 Yehova wazungulira anthu ake+

Ngati mmene mapiri azungulirira Yerusalemu,+

Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

 3 Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala+ padziko limene olungama analandira monga cholowa chawo,

Kuti olungamawo asatambasule dzanja lawo ndi kuchita choipa.+

 4 Inu Yehova, chitirani zabwino anthu abwino,+

Anthu owongoka mtima.+

 5 Koma anthu obwerera kunjira zawo zokhotakhota,+

Yehova adzawapereka ku chilango pamodzi ndi ochita zopweteka anzawo.+

Ndipo mu Isiraeli mudzakhala mtendere.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

126 Pamene Yehova anasonkhanitsa ndi kubwezeretsa ogwidwa ukapolo a Ziyoni,+

Tinakhala ngati tikulota.+

 2 Pa nthawiyo tinaseka kwambiri,+

Ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa.+

Pamenepo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:+

“Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+

 3 Yehova watichitira zazikulu.+

Tasangalala.+

 4 Sonkhanitsani ndi kubwezeretsa gulu lathu logwidwa ukapolo inu Yehova,+

Ngati mmene mumabwezeretsera madzi m’mitsinje ya ku Negebu.+

 5 Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu,+

Adzakolola akufuula mosangalala.+

 6 Amene akupita kumunda akulira,+

Atasenza thumba lodzaza mbewu,+

Adzabwerako akufuula mosangalala,+

Atasenza mtolo wake wa zokolola.+

Nyimbo ya Solomo Yokwerera Kumzinda.

127 Yehova akapanda kumanga nyumba,+

Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+

Yehova akapanda kulondera mzinda,+

Alonda amakhala maso pachabe.+

 2 Anthu inu mukudzuka m’mawa pachabe,+

Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,+

Mukudya chakudya chimene mwachipeza movutikira.+

Koma Mulungu amapereka tulo kwa wokondedwa wake.+

 3 Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+

Chipatso cha mimba ndicho mphoto.+

 4 Ana a bambo wachinyamata+

Ali ngati mivi m’dzanja la mwamuna wamphamvu.+

 5 Wodala ndi mwamuna wamphamvu amene wadzaza+ kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.

Abambo oterowo sadzachita manyazi,+

Pakuti anawo adzalankhula ndi adani pachipata.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

128 Wodala ndi aliyense woopa Yehova,+

Amene amayenda m’njira za Mulungu.+

 2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+

Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+

 3 Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobala zipatso+

Mkati mwa nyumba yako.

Ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya maolivi+ kuzungulira tebulo lako.

 4 Taonani! Mwamuna aliyense wamphamvu woopa Yehova+

Adzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+

 5 Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni.+

Komanso usangalale ndi zinthu zabwino za mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+

 6 Ndipo uone ana a ana ako.+

Mtendere ukhale pa Isiraeli.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

129 “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,”+

Isiraeli anene kuti,+

 2 “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,+

Koma sanandigonjetse.+

 3 Olima ndi ng’ombe andilima pamsana.*+

Iwo alima mizere italiitali.”

 4 Yehova ndi wolungama.+

Iye waduladula zingwe za oipa.+

 5 Onse odana ndi Ziyoni,+

Adzachita manyazi ndipo adzatembenuka ndi kubwerera okha.+

 6 Adzakhala ngati udzu wanthete womera padenga,+

Umene umauma asanauzule,+

 7 Umene wokolola sanadzaze nawo manja ake,+

Ngakhalenso aliyense amene akunyamula mitolo ya zokolola sanadzaze nawo thumba lake la pachifuwa.

 8 Anthu odutsa nawonso sananene kuti:

“Madalitso a Yehova akhale nanu anthu inu.+

Takudalitsani m’dzina la Yehova.”+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

130 Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+

 2 Imvani mawu anga Yehova.+

Makutu anu amve mawu anga ochonderera.+

 3 Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa,+

Ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+

 4 Inu mumakhululukiradi,+

Kuti anthu akuopeni.+

 5 Ndayembekezera thandizo lanu, inu Yehova. Moyo wanga wayembekezera thandizo lanu.+

Ine ndayembekezera mawu anu.+

 6 Ndayembekezera Yehova+

Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+

Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.+

 7 Isiraeli ayembekezere Yehova,+

Pakuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha.+

Iye ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu ake.+

 8 Iye adzawombola Isiraeli ku zolakwa zake zonse.+

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.

131 Inu Yehova, mtima wanga sunadzikweze,+

Maso anga si onyada.+

Sindinafune zinthu zapamwamba kwambiri,+

Kapena zinthu zodabwitsa kwambiri.+

 2 Ine ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi.+

Ndakhala ngati mwana amene wangosiya kumene kuyamwa, amene ali m’manja mwa mayi ake.+

Ndakhala ngati mwana amene wangosiya kumene kuyamwa.+

 3 Isiraeli ayembekezere Yehova,+

Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

132 Inu Yehova, kumbukirani Davide,+

Kumbukirani masautso ake onse.+

 2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,+

Analonjeza kwa Wamphamvu+ wa Yakobo kuti:+

 3 “Sindilowa m’nyumba yanga.+

Sindigona pabedi langa.+

 4 Maso anga saona tulo,+

Ndipo sindilola maso anga owala kuwodzera,+

 5 Kufikira Yehova nditamupezera nyumba,+

Kufikira nditapeza chihema chachikulu cha Wamphamvu wa Yakobo.”+

 6 Taonani! Tamva za Likasa* ku Efurata,+

Talipeza kunkhalango.+

 7 Tiyeni tilowe m’chihema chake chachikulu.+

Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+

 8 Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe kumalo anu okhalamo,+

Inu pamodzi ndi Likasa+ limene mumasonyezera mphamvu zanu.+

 9 Ansembe anu avale chilungamo,+

Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.+

10 Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,+

Musakane kuona nkhope ya wodzozedwa wanu.+

11 Yehova walumbira kwa Davide,+

Ndithudi sadzabweza mawu ake akuti:+

“Ndidzaika pampando wako wachifumu+

Chipatso cha mimba yako.+

12 Ana ako akadzasunga pangano langa+

Ndi zikumbutso zanga zimene ndidzawapatsa,+

Ngakhalenso ana awo+

Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+

13 Yehova wasankha Ziyoni,+

Ndipo amafunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye amati:+

14 “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka muyaya.+

Ndidzakhala mmenemu, pakuti ndimafunitsitsa kukhala m’malo amenewa.+

15 Ndithu ndidzadalitsa chakudya chake.+

Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+

16 Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+

Ndipo anthu ake okhulupirika adzafuula ndithu mokondwera.

17 Ku Ziyoniko ndidzakulitsa nyanga* ya Davide.+

Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+

18 Adani ake ndidzawaveka manyazi,+

Koma ufumu*+ wake udzapita patsogolo.”+

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.

133 Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri

Abale akakhala pamodzi mogwirizana!+

 2 Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu,+

Amene akutsikira kundevu,

Ndevu za Aroni,+

Amenenso akuyenderera mpaka m’khosi la zovala zake.+

 3 Zili ngati mame+ a ku Herimoni,+

Amene akutsikira pamapiri a ku Ziyoni.+

Pakuti Yehova analamula dalitso kukhala kumeneko,+

Walamulanso kuti kukhale moyo mpaka kalekale.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

134 Tamandani Yehova,+

Inu nonse atumiki a Yehova,+

Inu amene mumaimirira m’nyumba ya Yehova usiku.+

 2 Pamene mukupemphera mutakweza manja anu, muzikhala oyera,+

Ndipo tamandani Yehova.+

 3 Yehova, amene ndiye Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+

Akudalitseni ali ku Ziyoni.+

135 Tamandani Ya, anthu inu!+

Tamandani dzina la Yehova,+

Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+

 2 Inu amene mukuimirira m’nyumba ya Yehova,+

M’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+

 3 Tamandani Ya, pakuti Yehova ndi wabwino.+

Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti kuchita zimenezi n’kosangalatsa.+

 4 Ya wadzisankhira Yakobo,+

Wadzisankhira Isiraeli kukhala chuma chake chapadera.+

 5 Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu,+

Ndipo Ambuye wathu ndi woposa milungu ina yonse.+

 6 Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+

Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+

 7 Amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+

Iye anapanganso zipata zotulukirapo mvula.+

Amachititsa mphepo kutuluka m’nkhokwe zake.+

 8 Wochita zimenezi ndiye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,+

Anapha ana a anthu ngakhalenso ana a nyama.+

 9 Anasonyeza zizindikiro ndi kuchita zozizwitsa pakati pako Iguputo iwe,+

Anachita zimenezo kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+

10 Amene anachita zimenezi ndi amene anakantha mitundu yambiri+

Ndi kupha mafumu amphamvu.+

11 Anaphanso Sihoni mfumu ya Aamori+

Ndi Ogi mfumu ya Basana,+

Ndipo anafafaniza maufumu onse a ku Kanani.+

12 Dziko lawo analipereka kukhala cholowa,+

Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+

13 Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.+

Inu Yehova, dzina lanu* lidzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

14 Pakuti Yehova adzaweruzira anthu ake mlandu,+

Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+

15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+

Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+

16 Pakamwa ali napo koma salankhula.+

Maso ali nawo koma saona.+

17 Makutu ali nawo koma satha kumva.+

Komanso m’mphuno mwawo mulibe mpweya.+

18 Amene amawapanga adzafanana nawo,+

Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+

19 Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova.+

Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova.+

20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+

Inu oopa Yehova, tamandani Yehova.+

21 Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+

Atamandidwe mu Ziyoni.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

136 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino:+

Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 2 Yamikani Mulungu wa milungu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 3 Yamikani Mbuye wa ambuye:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 4 Yamikani Wochita zodabwitsa ndiponso ntchito zazikulu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 5 Yamikani amene anapanga kumwamba mwanzeru:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 6 Yamikani woyala dziko lapansi pamwamba pa madzi:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 7 Yamikani wopanga zounikira zazikulu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 8 Amenenso anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

 9 Amene anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira pamodzi usiku:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

10 Yamikani amene anakantha Aiguputo mwa kupha ana awo oyamba kubadwa:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

11 Yamikani amene anatulutsa Aisiraeli pakati pawo:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

12 Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.

13 Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

14 Amenenso anachititsa Isiraeli kudutsa pakati pake:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

15 Amenenso anakutumulira Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiira:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

16 Yamikani amene anayendetsa anthu ake m’chipululu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

17 Yamikani amene anapha mafumu amphamvu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

18 Amenenso anapha mafumu olemekezeka:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

19 Iye anapha Sihoni mfumu ya Aamori:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

20 Anaphanso Ogi mfumu ya Basana:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

21 Ndipo dziko lawo analipereka kwa anthu ake kukhala cholowa:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

22 Cholowa cha Isiraeli mtumiki wake:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

23 Iye amene anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

24 Amene anatipulumutsa mobwerezabwereza kuchokera m’manja mwa adani athu:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

25 Amenenso amapereka chakudya kwa zamoyo zonse:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

26 Yamikani Mulungu wakumwamba:+

Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

137 Tinakhala pansi+ m’mphepete mwa mitsinje ya ku Babulo,+

Ndipo tinalira titakumbukira Ziyoni.+

 2 Tinapachika azeze athu+

Pamitengo ya msondodzi.+

 3 Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+

Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati:

“Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+

 4 Tingaimbe bwanji nyimbo ya Yehova+

M’dziko lachilendo?+

 5 Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,+

Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.

 6 Lilime langa limamatire m’kamwa mwanga+

Ngati sindingakukumbukire,+

Ngati sindingakweze iwe Yerusalemu

Pamwamba pa chilichonse chimene chimandikondweretsa.+

 7 Inu Yehova, kumbukirani+ zimene ana a Edomu+ ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa,+

Iwo anati: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni mpaka pamaziko ake!”+

 8 Iwe mwana wamkazi wa Babulo, amene udzafunkhidwa,+

Wodala ndi amene adzakubwezera+

Zimene iwe watichitira.+

 9 Wodala ndi iye amene adzagwira ana ako ndi kuwaphwanya zidutswazidutswa+

Mwa kuwawombetsa pathanthwe.

Salimo la Davide.

138 Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+

Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu ina.+

 2 Ndidzawerama nditayang’ana kukachisi wanu woyera,+

Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+

Chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha+ ndi choonadi chanu.+

Pakuti malonjezo+ amene munawachita m’dzina lanu ndi aakulu ndithu. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezowo n’kwakukulu koposa.+

 3 Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+

Munandilimbitsa mtima ndi kundipatsa mphamvu.+

 4 Mafumu onse a padziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+

Pakuti adzakhala atamva mawu a pakamwa panu.

 5 Ndipo iwo adzaimba za njira za Yehova,+

Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+

 6 Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+

Koma wodzikuza samuyandikira.+

 7 Ndikakhala pa masautso, inu mudzandisunga wamoyo.+

Mudzatambasula dzanja lanu chifukwa cha mkwiyo wa adani anga,+

Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.+

 8 Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.+

Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+

Musasiye ntchito ya manja anu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

139 Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+

 2 Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimirira.+

Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+

 3 Mumandidziwa bwino pamene ndikuyenda komanso pamene ndikugona,+

Ndipo njira zanga zonse mukuzidziwa bwino.+

 4 Ndisananene kanthu,+

Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+

 5 Mwandizungulira,

Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.

 6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+

Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+

 7 Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,+

Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+

 8 Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko.+

Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.+

 9 Ngati ndingakwere pamapiko+ a m’bandakucha,

Kuti ndikakhale m’nyanja ya kutali kwambiri,+

10 Kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,+

Dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+

11 Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undipeze mofulumira!”+

Pamenepo mdima udzasanduka kuwala pa ine.+

12 Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+

Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+

Mdima udzangokhala ngati kuwala.+

13 Inu munapanga impso zanga,+

Ndipo munali kunditchinga m’mimba mwa mayi anga.+

14 Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+

Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+

Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+

15 Mafupa anga sanali obisika kwa inu+

Pamene munali kundipanga m’malo obisika,+

Pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri+ padziko lapansi.

16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+

Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.

M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+

Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.

17 Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri,+ inu Mulungu,

Ndipo ndi ochuluka zedi.+

18 Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+

Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.+

19 Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha woipa.+

Pamenepo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi+ akanandichokera,

20 Anthu amene amanena zam’mutu mwawo zotsutsana ndi inu.+

Adani anuwo+ agwiritsa ntchito dzina lanu mosasamala.+

21 Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu kwambiri,+

Ndipo anthu okupandukirani ndimanyansidwa nawo.+

22 Ndimadana nawo kwambiri.+

Kwa ine akhala adani enieni.+

23 Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.+

Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere,+

24 Ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa,+

Ndipo munditsogolere m’njira+ yamuyaya.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

140 Inu Yehova, ndilanditseni kwa anthu oipa.+

Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa,+

 2 Anthu amene amakonza chiwembu mumtima mwawo,+

Amene amandiukira tsiku lonse ngati mmene zimakhalira pankhondo.+

 3 Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+

M’milomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ [Seʹlah.]

 4 Inu Yehova, ndithandizeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+

Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa.+

Nditetezeni kwa anthu amene andikonzera chiwembu kuti andikankhe ndi kundigwetsa.+

 5 Anthu odzikweza anditchera msampha.+

Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+

Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.]

 6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.+

Tcherani khutu, inu Yehova, ku mawu anga ochonderera.”+

 7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,+ mpulumutsi wanga wamphamvu,+

Mwatchinga ndi kuteteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+

 8 Inu Yehova, munthu woipa musam’patse zimene mtima wake umafuna.+

Musalole kuti chiwembu chawo chitheke chifukwa angadzikweze.+ [Seʹlah.]

 9 Kunena za anthu amene andizungulira,+

Zoipa zotuluka pakamwa pawo ziphimbe mitu yawo.+

10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+

Muwachititse kugwera m’moto+ ndi m’madzi akuya kuti asanyamukenso.+

11 Munthu wolankhula zazikulu* asakhazikike padziko lapansi.+

Zoipa zisakesake munthu wochita zachiwawa ndipo zimukanthe mobwerezabwereza.+

12 Ndikudziwa bwino kwambiri kuti Yehova adzazengera+

Mlandu anthu osautsika. Iye adzachitira chilungamo anthu osauka.+

13 Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.+

Anthu owongoka mtima adzakhalabe pamaso panu.+

Nyimbo ya Davide.

141 Inu Yehova, ine ndakuitanani.+

Bwerani kwa ine mofulumira.+

Tcherani khutu pamene ndikukuitanani.+

 2 Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza+ pamaso panu,+

Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+

 3 Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.+

Ikani wolondera patsogolo pa milomo yanga.+

 4 Musachititse mtima wanga kukonda choipa chilichonse,+

Kuti ndisamachite zinthu zoipa zonditchukitsa,+

Pamodzi ndi amene amachita zinthu zopweteka anzawo,+

Kuti ndisadye chakudya chawo chapamwamba.+

 5 Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+

Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+

Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+

Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+

 6 Oweruza awo awagwetsera pansi m’mphepete mwa thanthwe,+

Koma anthu awo amva zonena zanga ndipo aona kuti ndi zabwino.+

 7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,

Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+

 8 Koma ine maso anga ali pa inu+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+

Ndathawira kwa inu.+

Musalole kuti moyo wanga uwonongeke.+

 9 Nditetezeni kuti ndisagwidwe pamsampha umene anditchera,+

Kuti ndisakodwe ndi makhwekhwe a anthu ochita zopweteka anzawo.+

10 Oipa onse adzagwera m’maukonde awo omwe,+

Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kukhala kuphanga.+

142 Ndinafuulira Yehova kuti andithandize.+

Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima.+

 2 Ndinapitirizabe kumukhuthulira nkhawa zanga.+

Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga.+

 3 Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka.

Pamenepo, munadziwa njira yanga.+

Adani anga anditchera msampha+

M’njira imene ndikuyenda.+

 4 Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muone

Kuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+

Ndilibenso malo othawirako,+

Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+

 5 Ndinafuula kwa inu kuti mundithandize, inu Yehova.+

Ndinanena kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga,+

Gawo langa+ m’dziko la amoyo.”+

 6 Mvetserani kulira kwanga kochonderera,+

Pakuti ndasautsika koopsa.+

Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+

Pakuti iwo ndi amphamvu kuposa ine.+

 7 Nditulutseni mundende ya mdima+

Kuti nditamande dzina lanu.+

Chititsani kuti anthu olungama asonkhane ndi kundizungulira,+

Chifukwa mumandichitira zabwino.+

Nyimbo ya Davide.

143 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+

Tcherani khutu pamene ndikuchonderera.+

Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.+

 2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,+

Pakuti palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+

 3 Mdani akufunafuna moyo wanga,+

Iye waupondaponda pafumbi.+

Wandichititsa kukhala m’malo a mdima ngati anthu amene anafa kalekale.+

 4 Mtima wanga+ walefuka,

Ndipo wachita dzanzi.+

 5 Ndakumbukira masiku akale.+

Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+

Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+

 6 Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.+

Moyo wanga uli ngati dziko louma limene likulakalaka kuti muthetse ludzu lake.+ [Seʹlah.]

 7 Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova.+

Mphamvu zanga zatha.+

Musandibisire nkhope yanu,+

Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+

 8 M’mawa ndichititseni kumva za kukoma mtima kwanu kosatha,+

Pakuti ndimadalira inu.+

Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo,+

Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu.+

 9 Ndilanditseni kwa adani anga, inu Yehova.+

Ine ndathawira kwa inu.+

10 Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+

Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+

Mzimu wanu ndi wabwino.+

Unditsogolere m’dziko la olungama.+

11 Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo+ chifukwa cha dzina lanu.+

Chotsani moyo wanga m’masautso+ monga mwa chilungamo chanu.+

12 Adani anga muwakhalitse chete monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+

Ndipo muwononge onse ondichitira zoipa,+

Pakuti ine ndine mtumiki wanu.+

Salimo la Davide.

144 Atamandike Yehova Thanthwe langa,+

Amene akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+

Amenenso akuphunzitsa zala zanga kumenyana ndi adani anga.

 2 Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo,+

Malo anga okwezeka ndi Wopereka chipulumutso,+

Chishango+ changa ndi malo anga othawirako.+

Iye amandigonjetsera mitundu ya anthu.+

 3 Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizire?+

Kodi mwana wa munthu wochokera kufumbi+ ndani kuti mumuwerengere?

 4 Munthu amafanana ndi mpweya wotuluka m’mphuno.+

Masiku ake ali ngati mthunzi wongodutsa.+

 5 Inu Yehova, weramitsani kumwamba kuti mutsike.+

Khudzani mapiri kuti afuke utsi.+

 6 Ng’animitsani mphezi kuti muwabalalitse.+

Tumizani mivi yanu kuti muwasokoneze.+

 7 Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.+

Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’madzi ambiri.+

Mundilanditse m’manja mwa anthu achilendo,+

 8 Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+

Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+

 9 Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+

Ndidzaimba nyimbo yokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10.+

10 Ndidzaimbira inu amene mumapulumutsa mafumu,+

Amene mumalanditsa ine Davide mtumiki wanu ku lupanga lovulaza.+

11 Ndimasuleni ndi kundilanditsa m’manja mwa anthu achilendo,+

Anthu amene amalankhula zinthu zonama,+

Amenenso dzanja lawo lamanja limachita zachinyengo.+

12 Anthuwo amanena kuti: “Ana athu aamuna, mu unyamata wawo, ali ngati mitengo imene yangokhwima kumene,+

Ndipo ana athu aakazi ali ngati mizati yapakona yosemedwa mwaluso ya m’nyumba ya mfumu.

13 Nkhokwe zathu ndi zodzaza ndi zakudya zosiyanasiyana.+

Nkhosa zathu zikuswana kukhala masauzandemasauzande. Nkhosa imodzi ikukhala masauzande 10 m’misewu.

14 Ng’ombe zathu zili ndi bere, sizikuvulala kapena kubereka ana akufa,+

Ndipo palibe munthu amene akulira m’mabwalo athu.+

15 Odala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira.”

Ayi, koma odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+

Nyimbo yotamanda Mulungu. Salimo la Davide.

א [ʼAʹleph]

145 Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+

Ndipo ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

ב [Behth]

 2 Ndidzakutamandani tsiku lonse.+

Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

ג [Giʹmel]

 3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+

Ndipo ukulu wake ndi wosasanthulika.+

ד [Daʹleth]

 4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo,+

Ndipo adzasimba za zochita zanu zamphamvu.+

ה [Heʼ]

 5 Ndidzasinkhasinkha za ulemerero wanu waukulu+

Ndi nkhani zokhudza ntchito zanu zodabwitsa.+

ו [Waw]

 6 Anthu adzanena za zochita zanu zamphamvu ndi zochititsa mantha.+

Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.+

ז [Zaʹyin]

 7 Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+

Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+

ח [Chehth]

 8 Yehova ndi wachisomo ndi wachifundo,+

Wosakwiya msanga ndi wosonyeza kukoma mtima kosatha komanso kwakukulu.+

ט [Tehth]

 9 Yehova amakomera mtima aliyense,+

Ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.+

י [Yohdh]

10 Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+

Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+

כ [Kaph]

11 Iwo adzanena za ulemerero wa ufumu wanu.+

Ndi kulankhula za mphamvu zanu,+

ל [Laʹmedh]

12 Kuti ana a anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+

Ndi kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+

מ [Mem]

13 Ufumu wanu ndi ufumu umene udzakhalapobe mpaka kalekale.+

Ulamuliro wanu udzakhalapobe ku mibadwo yonse.+

ס [Saʹmekh]

14 Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa,+

Ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.+

ע [ʽAʹyin]

15 Zolengedwa zonse zimayang’ana kwa inu mwachiyembekezo,+

Ndipo mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+

פ [Peʼ]

16 Mumatambasula dzanja lanu+

Ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.+

צ [Tsa·dhehʹ]

17 Yehova ndi wolungama m’njira zake zonse,+

Ndipo ndi wokhulupirika m’ntchito zake zonse.+

ק [Qohph]

18 Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.+

Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi,+

ר [Rehsh]

19 Ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo,+

Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.+

ש [Shin]

20 Yehova amayang’anira onse omukonda,+

Koma oipa onse adzawafafaniza.+

ת [Taw]

21 Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova,+

Ndipo anthu onse atamande dzina lake loyera mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

146 Tamandani Ya, anthu inu!+

Iwe moyo wanga, tamanda Yehova.+

 2 Ndidzatamanda Yehova pamene ndili moyo.+

Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.+

 3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka,+

Kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso.+

 4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+

Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+

 5 Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo,+

Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+

 6 Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+

Nyanja ndi zonse zili mmenemo.+

Wosunga choonadi mpaka kalekale.+

 7 Iye ndi Woperekera chiweruzo anthu ochitiridwa chinyengo,+

Wopereka chakudya kwa anthu anjala.+

Yehova amamasula anthu omangidwa.+

 8 Yehova amatsegula maso a anthu akhungu.+

Yehova amaweramutsa anthu owerama chifukwa cha masautso.+

Yehova amakonda anthu olungama.+

 9 Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.+

Amathandiza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.+

Koma njira+ ya anthu oipa amaichititsa kukhala yovuta kuyendamo.+

10 Yehova adzakhala mfumu mpaka kalekale,+

Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala mfumu ku mibadwomibadwo.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

147 Tamandani Ya, anthu inu,+

Pakuti kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino,+

Ndipo n’kosangalatsa. Kumutamanda n’koyenera.+

 2 Yehova akumanga Yerusalemu.+

Anthu okhala mu Isiraeli amene anabalalika akuwasonkhanitsanso pamodzi.+

 3 Iye amachiritsa+ anthu osweka mtima,+

Ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.+

 4 Amawerenga nyenyezi zonse,+

Ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.+

 5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.+

Nzeru zake zilibe malire.+

 6 Yehova amathandiza anthu ofatsa,+

Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.+

 7 Imbirani Yehova molandizana mawu nyimbo zomuyamikira anthu inu.+

Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda ndi zeze.+

 8 Muimbireni Iye amene amaphimba mapiri ndi mitambo,+

Amene amakonza mvula kuti igwe padziko lapansi,+

Amenenso amameretsa udzu wobiriwira m’mapiri.+

 9 Iye amapatsa zilombo chakudya chawo,+

Amapatsanso ana a makwangwala chakudya chimene amalirira.+

10 Iye sadalira mphamvu za hatchi,+

Kapena liwiro la miyendo ya munthu.+

11 Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+

Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.+

12 Yamika Yehova,+ iwe Yerusalemu.

Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.+

13 Pakuti walimbitsa mipiringidzo ya zipata zako.

Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe.+

14 Iye akukhazikitsa mtendere m’dziko lako.+

Ndipo akupitirizabe kukukhutiritsa ndi tirigu wabwino koposa.+

15 Amatumiza mawu ake padziko lapansi,+

Ndipo mawu akewo amathamanga kwambiri.

16 Iye amapereka chipale chofewa kuti chikhale ngati ubweya wa nkhosa.+

Amamwaza mame oundana ngati kuti ndi phulusa.+

17 Amaponya madzi oundana ngati nyenyeswa za chakudya.+

Ndani angaime m’chisanu chake?+

18 Amatumiza mawu ake+ ndi kusungunula madzi oundanawo.

Amachititsa mphepo yake kuwomba,+

Ndipo madzi amayenda.

19 Amauza Yakobo mawu ake,+

Ndipo amauza Isiraeli malangizo+ ake ndi zigamulo zake.+

20 Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+

Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

148 Tamandani Ya, anthu inu!+

Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+

Mutamandeni inu okhala m’mwamba.+

 2 Mutamandeni, inu angelo ake onse.+

Mutamandeni, inu khamu lake lonse.+

 3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi.+

Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+

 4 Mutamandeni, inu kumwamba kwa m’mwambamwamba,+

Ndi inunso madzi okhala pamwamba pa miyamba.+

 5 Zonsezi zitamande dzina la Yehova,+

Pakuti iye analamula ndipo zinalengedwa.+

 6 Amazichititsa kukhalapobe kwamuyaya, ngakhalenso mpaka kalekale.+

Iye wazikhazikitsira lamulo, ndipo silidzatha.+

 7 Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,+

Inu zilombo za m’nyanja ndi inu nonse madzi akuya,+

 8 Inu moto ndi matalala, chipale chofewa ndi utsi wakuda bii,+

Iwe mphepo yamkuntho yokwaniritsa mawu ake.+

 9 Mutamandeni inu mapiri ndi inu nonse zitunda,+

Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+

10 Inu nyama zakutchire ndi inu nonse nyama zoweta,+

Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko.+

11 Mutamandeni inu mafumu a padziko lapansi+ ndi inu nonse mitundu ya anthu,

Inunso akalonga+ ndi inu nonse oweruza a padziko lapansi,+

12 Inu anyamata+ ndi inunso anamwali,+

Inu okalamba+ pamodzi ndi ana.+

13 Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+

Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+

Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+

14 Iye adzakweza nyanga* ya anthu ake.+

Adzachititsa kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,+

Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

149 Tamandani Ya, anthu inu!+

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+

Muimbireni nyimbo zomutamanda mu mpingo wa anthu ake okhulupirika.+

 2 Isiraeli asangalale ndi Womupanga Wamkulu,+

Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.+

 3 Atamande dzina lake mwa kuvina.+

Amuimbire nyimbo zomutamanda ndi maseche ndi zeze,+

 4 Pakuti Yehova amasangalala ndi anthu ake.+

Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+

 5 Anthu okhulupirika akondwere mu ulemerero.

Iwo aimbe mosangalala pamabedi awo.+

 6 Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,+

Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale m’manja mwawo,+

 7 Kuti abwezere anthu a mitundu ina,+

Ndi kudzudzula mitundu ya anthu,+

 8 Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,+

Ndi kumanga anthu awo olemekezeka m’matangadza achitsulo.

 9 Kuti awaweruze motsatira chigamulo cholembedwa.+

Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

150 Tamandani Ya, anthu inu!+

Tamandani Mulungu m’malo ake oyera.+

Mutamandeni m’mlengalenga mmene mumasonyeza mphamvu zake.+

 2 Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+

Mutamandeni mogwirizana ndi ukulu wake wosaneneka.+

 3 Mutamandeni mwa kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+

Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe ndi zeze.+

 4 Mutamandeni ndi maseche+ ndi gule wovina mozungulira.+

Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+

 5 Mutamandeni ndi chinganga cha mawu osangalatsa.+

Mutamandeni ndi chinganga cha mawu amphamvu.+

 6 Chopuma chilichonse chitamande Ya.+

Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu akuti “Masalimo” amatanthauza “Nyimbo Zotamanda.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

“Seʹlah” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo kapena ndakatulo. Tanthauzo lake lenileni silikudziwika.

“Nehiloti” ndi mawu achiheberi ndipo tanthauzo lake lenileni silikudziwika. N’kutheka kuti ndi dzina la chipangizo choimbira mochita kuuziramo mpweya kapena dzina la nyimbo yoimba motsagana ndi zipangizo zoimbira.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

N’kutheka kuti mawu amene tawamasulira kuti “chapansipansi” akutanthauza kuti anali kuimba nyimbo imeneyi motsitsa kapena mwabesi.

Onani Zakumapeto 5.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyimbo yoimba polira” silikudziwika, koma mwina mawu amenewo angatanthauze nyimbo yoimba mokhudzidwa mtima kwambiri. Kaimbidwe kake kangasonyeze kuti moyo wa munthuyo uli pangozi, akufuula kupempha thandizo, kapena akukondwera ndipo akutamanda winawake.

“Gititi” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.

Kapena kuti “angelo.”

“Mutilabeni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake lenileni silikudziwika. Koma omasulira ena anamasulira mawuwa kuti, “yonena za imfa ya mwana wamwamuna.”

“Higayoni” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 6:Kamutu.

Mawu ake enieni, “m’badwo.”

“Mikitamu” ndi mawu amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.

Mawu ake enieni, “adzikuta ndi mafuta awo omwe.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Kapena kuti “mapiko a mphepo.”

Mawu ake enieni, “amamangirira zolimba mphamvu m’chiuno mwanga.”

Kapena kuti “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”

Ena amati “n’zonzuna.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Mawu ake enieni, “ana a amphamvu.”

“Madzi” amenewa akutanthauza “mvula yamkuntho.”

Kapena kuti “pamwamba pa nyanja yaikulu ya kumwamba.”

Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”

Ena amati “saka.”

Onani Zakumapeto 4.

“Masikili” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika. N’kutheka kuti amatanthauza “ndakatulo imene munthu amanena posinkhasinkha.”

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.

Zikuoneka kuti ili ndi dzina laudindo la Mfumu Akisi. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa Ge 20:2.

“Yedutuni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika.

Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.

Mawu ake enieni, “chinthu chopanda pake.”

Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

N’kutheka kuti “Maluwa” chinali chipangizo choimbira cha zingwe 6.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

N’kutheka kuti mawu akuti “zishango” akunena olamulira kapena oteteza anthu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “mafupa.”

Kapena kuti “mzimu.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

“Mahalati” ndi mawu achiheberi. N’kutheka kuti ndi mawu okhudzana ndi nyimbo, mwina okhudzana ndi luso la kaimbidwe.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 39:Kamutu.

Pa nthawi ya Mfumu Davide, Aisiraeli anali ndi maulonda a usiku atatu. Ulonda woyamba unkayamba 6 koloko madzulo mpaka 10 koloko usiku. Ulonda wachiwiri unkayamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku, ndipo ulonda wachitatu unkayamba 2 koloko usiku mpaka 6 koloko m’mawa.

Mawu ake enieni, “mudzaphimba.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Mawu ake enieni, “Ya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.

Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina” silidziwika. Ena amati tanthauzo lake ndi “akazembe.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 45:Kamutu.

Zikuoneka kuti “dzenje” limeneli ndi manda.

Mawu ake enieni, “chiuno.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti alandire madalitso amenewo.

Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Kapena kuti “ng’ona.”

M’Malemba achiheberi mulibe mawu akuti “Mulungu akuti,” koma aikidwapo pofuna kusonyeza amene akulankhula m’mavesi 2 ndi 3.

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Onani mawu a m’munsi pa vesi 2.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Mawu ake enieni, “kuphimba.”

Mawu ake enieni, “kuphimba.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 45:Kamutu.

Onani Sl 60:Kamutu.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 8:Kamutu.

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 8:Kamutu.

Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”

Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 53:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo kapena Farao.

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”

Kapena kuti “musanamve zowawa ngati za pobereka pokhazikitsa dziko lapansi.”

Zikuoneka kuti usiku anali kuugawa zigawo zitatu za ulonda, kuyambira pamene dzuwa lalowa mpaka kutuluka. Ulonda uliwonse unali pafupifupi maola anayi malinga ndi nyengo ya pachaka.

Kapena kuti “machimo amene tinachita mosadziwa.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Kapena kuti “imvani kupweteka kwambiri.”

Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”

“Mphalasa” ndi lipenga lopangidwa ndi nyanga ya nkhosa.

Kapena kuti “patsindwi.”

Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”

Mawu ake enieni, “anthu amene adzalengedwe.”

Kapena kuti “ng’ona.”

Kapena kuti “Aleluya.”

Kapena kuti “Zikhale momwemo!”

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Kapena kuti “phindu lopezeka mwachinyengo pamalonda.”

Mawu ake enieni, “ndafewetsa nkhope yanu.”

Mawu ake enieni, “moyo wanga uli m’dzanja langa.”

Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.

Zikuoneka kuti apa akunena za nkhanza zimene mitundu ina yodana nawo inawachitira.

Kapena “Chihema.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Mawu ake enieni, “chisoti chachifumu.”

Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”

Kapena kuti “woneneza.” Mawu ake enieni ndi “munthu wa lilime.”

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.

Onani Zakumapeto 4.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena