Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Jeremiah 1:1-52:34
  • Yeremiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yeremiya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yeremiya

Yeremiya*

1 Mawu a Yeremiya+ mwana wa Hilikiya,* mmodzi wa ansembe a ku Anatoti,+ m’dera la Benjamini.+ 2 Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova m’masiku a Yosiya+ mwana wa Amoni.+ Yosiya anali mfumu ya Yuda, ndipo Yeremiya analandira mawuwo m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiyayo.+ 3 Mawuwo anapitiriza kufika kwa Yeremiya m’masiku a Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, mpaka m’chaka cha 11, kumapeto kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, pamene anthu a mu Yerusalemu anatengedwa kupita ku ukapolo m’mwezi wachisanu.*+

4 Ndiyeno Yehova anayamba kulankhula nane kuti: 5 “Ndisanakuumbe m’mimba,+ ndinakudziwa,+ ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti uchite ntchito yopatulika.+ Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”

6 Koma ine ndinati: “Haa! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindingathe kulankhula+ chifukwa ndine mwana.”+

7 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana.’ Koma upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.+ 8 Usachite mantha chifukwa cha nkhope zawo,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’”+

9 Pamenepo Yehova anatambasula dzanja lake ndi kukhudza pakamwa panga.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Ndaika mawu anga m’kamwa mwako.+ 10 Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu,+ kuti uzule, ugwetse,+ uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kubzala.”+

11 Ndiyeno Yehova anapitirizabe kulankhula nane, ndipo anati: “Ukuona chiyani Yeremiya?”

Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphukira ya mtengo wa amondi.”*

12 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Waona bwino, chifukwa ndikhalabe wogalamuka* kuti ndikwaniritse mawu anga.”+

13 Kenako Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti: “Ukuona chiyani?”

Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphika wakukamwa kwakukulu umene uli pamoto, ndipo motowo aupemerera kuti uyake kwambiri. Mphikawo wafulatira kumpoto.”

14 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Tsoka lidzamasulidwa kuchokera kumpoto ndipo lidzagwera anthu onse okhala m’dzikoli.+ 15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+ 16 Ndipo ine ndidzapereka zigamulo zanga pa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda chifukwa cha zoipa zawo zonse,+ pakuti iwo andisiya ine+ ndipo amafukiza nsembe zautsi kwa milungu ina+ ndi kugwadira ntchito za manja awo.’+

17 “Koma iwe umange m’chiuno+ ndipo upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha chifukwa cha iwo,+ kuopera kuti ndingakuchititse kugwidwa ndi mantha pamaso pawo. 18 Koma ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa+ kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+ Ndithu kuti mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikoli asakugonjetse.+ 19 Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe+ kuti ndikulanditse.’”+

2 Ndiyeno Yehova anandiuzanso+ kuti: 2 “Pita, ukafuule m’makutu a anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Ndikukumbukira bwino kwambiri kukoma mtima kosatha kumene unali nako pamene unali wachinyamata,+ chikondi chimene unali nacho pa nthawi imene unali kulonjezedwa kukwatiwa,+ ndi kuti unanditsatira poyenda m’chipululu, m’dziko losabzalidwa kalikonse.+ 3 Isiraeli anali wopatulika kwa Yehova,+ ndipo anali zipatso zoyambirira kwa Iye.”’+ ‘Anthu onse ofuna kumumeza anali kukhala ndi mlandu+ ndipo tsoka linali kuwagwera,’ watero Yehova.”+

4 Tamverani mawu a Yehova, inu a m’nyumba ya Yakobo+ ndi inu nonse mafuko a m’nyumba ya Isiraeli.+ 5 Yehova wanena kuti: “Kodi makolo anu anandipeza ndi chiyani chosalungama+ kuti akhale patali ndi ine?+ Anandipeza ndi chiyani kuti ayambe kutsatira fano lopanda pake+ iwonso n’kukhala anthu opanda pake?+ 6 Iwo sananene kuti, ‘Ali kuti Yehova, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo,+ amene anatitsogolera m’chipululu,+ m’dera lam’chipululu lodzaza ndi mayenje, m’dziko lopanda madzi+ ndi la mdima wandiweyani,+ dziko limene simunadutse munthu aliyense komanso mmene simunali kukhala munthu aliyense?’

7 “M’kupita kwa nthawi, ndinakulowetsani m’dziko la minda ya zipatso kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino za m’dzikolo,+ koma munalowa m’dziko langa ndi kuliipitsa. Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+ 8 Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Ndipo anthu ophunzitsa chilamulo sanandidziwe.+ Abusa nawonso anaphwanya malamulo anga,+ ndipo aneneri anali kulosera m’dzina la Baala+ ndi kutsatira milungu yopanda phindu.+

9 “‘Choncho ndidzapitirizabe kulimbana nanu anthu inu,’+ watero Yehova, ‘ndipo ndidzalimbananso ndi ana a ana anu.’+

10 “‘Wolokerani ku Kitimu,+ m’mbali mwa nyanja, kuti muone. Tumizani anthu ku Kedara+ ndipo muganizire bwinobwino kuti muone ngati zoterezi zinachitikapo kumeneko.+ 11 Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+ 12 Yang’anitsitsani zimenezi modabwa, inu kumwamba, ndipo tsitsi lanu liimirire ndi mantha aakulu kwambiri,’ watero Yehova,+ 13 ‘chifukwa pali zinthu ziwiri zoipa zimene anthu anga achita: Iwo asiya ine+ kasupe wa madzi amoyo,+ ndipo akumba zitsime zawozawo, zitsime zong’ambika zimene sizingasunge madzi.’

14 “‘Isiraeli si mtumiki wanga+ komanso si kapolo wobadwira m’nyumba mwanga, si choncho kodi? Nanga n’chifukwa chiyani wafunkhidwa? 15 Mikango yamphamvu imamubangulira.+ Imamutulutsira mawu awo.+ Ndipo yapangitsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa kwa ena. Mizinda yake aiyatsa moto, choncho simukukhala munthu aliyense.+ 16 Ngakhale anthu a ku Nofi+ ndi ku Tahapanesi+ anawononga dziko lako.*+ 17 Kodi sunadzichitire wekha zimenezi mwa kusiya Yehova Mulungu wako+ pa nthawi imene anali kukuyendetsa m’njira yake?+ 18 Ndiyeno n’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira ya ku Iguputo+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Sihori?+ N’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira yopita kudziko la Asuri+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Firate? 19 Uphunzirepo kanthu pa kuipa kwako+ ndipo zochita zako zosakhulupirika zikudzudzule.+ Dziwa izi, ndipo ona kuti kusiya kwako Yehova Mulungu wako ndi chinthu choipa ndi chowawa.+ Iwe sundiopa ine,’+ watero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.+

20 “‘Ine ndinaphwanya goli lako kukhala zidutswazidutswa kalekale.+ Ndinadula zingwe zimene anakumanga nazo. Koma iwe unati: “Sindikutumikirani,” ndipo unagona motangadza+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ n’kumachita uhule+ pamenepo. 21 Koma ine ndinakubzala ngati mtengo wa mpesa wofiira, wabwino kwambiri.+ Mtengo wonsewo unali mbewu yeniyeni yabwino. Ndiye wandisinthira bwanji kukhala mphukira yachabechabe ya mtengo wa mpesa wachilendo?’+

22 “‘Koma ngakhale utasambira soda ndiponso sopo wambiri,+ cholakwa chako chidzaonekerabe ngati banga pamaso panga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 23 Unganene bwanji kuti, ‘Sindinadziipitse.+ Sindinatsatire mafano a Baala’?+ Ganizira bwinobwino njira yako m’chigwa.+ Onetsetsa zimene wachita. Wakhala ngati ngamila yaing’ono yaikazi imene ikungothamangira uku ndi uku. 24 Wakhala ngati mbidzi+ yaikazi yozolowera kukhala m’chipululu imene ili ndi chilakolako champhamvu, imene ikupuma mwawefuwefu.+ Ndani angaibweze pa nthawi yake yokweredwa? Mbidzi zamphongo zoifunafuna sizidzavutika kuipeza. M’mwezi wake wokweredwa zidzaipeza. 25 Samala kuti phazi lako lisakhale lopanda nsapato, ndi kuti usachite ludzu.+ Koma iwe unati, ‘Zimenezo ayi!+ Ine ndakondana ndi alendo+ ndipo ndidzawatsatira.’+

26 “Monga mmene mbala imachitira manyazi ikagwidwa, anthu a m’nyumba ya Isiraeli nawonso achita manyazi,+ iwowo, mafumu awo, akalonga awo, ansembe awo ndiponso aneneri awo.+ 27 Iwo akuuza mtengo kuti, ‘Ndinu bambo anga,’+ ndipo akuuza mwala kuti, ‘Ndinu amene munandibereka.’ Iwo andifulatira ndipo sanandisonyeze nkhope yawo.+ Koma tsoka likadzawagwera adzanena kuti, ‘Chonde, bwerani mudzatipulumutse!’+

28 “Kodi milungu yako imene wadzipangira ili kuti?+ Imeneyo ibwere kwa iwe ngati ingathe kukupulumutsa pa nthawi ya tsoka.+ Pakuti iwe Yuda, milungu yako yachuluka mofanana ndi mizinda yako.+

29 “‘Kodi n’chifukwa chiyani anthu inu mukupitiriza kundiimba mlandu?+ N’chifukwa chiyani nonsenu mwaphwanya malamulo anga?’+ watero Yehova. 30 Ndalanga ana anu aamuna koma sizinathandize.+ Iwo sanamve chilango* changa.+ Lupanga lanu lapha aneneri anu, ngati mkango umene ukupha anthu ambiri.+ 31 Inu anthu a m’badwo uwu, ganizirani mawu a Yehova.+

“Kodi ndangokhala ngati chipululu kwa Isiraeli+ kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? N’chifukwa chiyani anthu angawa anena kuti, ‘Takhala tikuyendayenda mmene tikufunira. Sitibwereranso kwa inu’?+ 32 Kodi namwali angaiwale zodzikongoletsera? Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wa pachifuwa? Koma anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+

33 “N’chifukwa chiyani mkazi iwe wakonza njira yako kuti ufunefune amuna oti akukonde? Pa chifukwa chimenechi wadziphunzitsa kuchita zinthu zoipa.+ 34 Komanso, pazovala zako papezeka madontho a magazi a anthu+ osauka osalakwa.+ Madontho a magaziwo sindinawapeze panyumba, ngati kuti anali kuthyola nyumbayo, koma ndawapeza pazovala zako zonse.+

35 “Koma iwe ukuti, ‘Ine ndilibe mlandu uliwonse. Ndithudi mkwiyo wake wandichokera.’+

“Tsopano ndikuyamba kukuimba mlandu chifukwa chonena kuti, ‘Sindinachimwe.’+ 36 N’chifukwa chiyani kusintha njira kwako ukukuona mopepuka?+ Udzachitanso manyazi ndi Iguputo+ monga mmene unachitira manyazi ndi Asuri.+ 37 Pa chifukwa chimenechi, udzayenda manja ako ali kumutu,+ chifukwa Yehova wakana zinthu zimene umazidalira ndipo sizidzakupindulitsa.”

3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+

Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+

Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+ 2 Kweza maso ako ndi kuona njira zodutsidwadutsidwa.+ Ndi pamalo ati pamene amuna sanakugonerepo?+ Unali kukhala m’mbali mwa njira kudikirira okondedwa ako, ngati mmene Mluya amakhalira m’chipululu.+ Ukuipitsa dzikoli ndi zochita zako zauhule komanso kuipa kwako.+ 3 Choncho mvula yamvumbi yasiya kugwa,+ ndipo mvula yomalizira siinagwe.+ Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.* Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+ 4 Tsopano wayamba kundiitana kuti, ‘Atate wanga,+ ndinu bwenzi langa lapamtima kuyambira pa unyamata wanga.+ 5 Kodi mukhala wokwiya mpaka kalekale?* Kapena kodi muzingoyang’anira machimo athu mpaka muyaya?’+ Taona! Iwe wanena ndi kuchita zinthu zoipa ndipo wapambana.”+

6 Yehova anapitiriza kulankhula nane m’masiku a Mfumu Yosiya kuti:+ “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita?+ Akupita kuphiri lililonse lalitali+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ kuti akachite uhule kumeneko.+ 7 Pambuyo poti wachita zinthu zonsezi, ine ndinamupempha mobwerezabwereza kuti abwerere kwa ine, koma iye sanabwerere.+ Ndipo Yuda anali kungoyang’anitsitsa zimene m’bale wake wachinyengoyo anali kuchita.+ 8 Nditaona zimenezo, ndinam’pitikitsa+ ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa chakuti Isiraeli wosakhulupirikayu anachita chigololo. Koma Yuda amene ndi m’bale wake wochita zachinyengo sanachite mantha ndipo nayenso anayamba kuchita uhule.+ 9 Iye anayamba kuchita uhule chifukwa choona nkhani imeneyi mopepuka. Anali kuipitsa dzikolo+ ndi kuchita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+ 10 Ngakhale kuti m’bale wake Yuda amene anali wochita zachinyengoyo anaona zonsezi, iye sanabwerere kwa ine ndi mtima wake wonse+ koma anangobwerera mwachiphamaso,’+ watero Yehova.”

11 Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Isiraeli wosakhulupirikayo wakhala wolungama kuposa Yuda wochita zachinyengoyo.+ 12 Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto+ kuti:

“‘Yehova wanena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyang’anani mokwiya anthu inu+ pakuti ndine wokhulupirika,”+ watero Yehova.+ “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.+ 13 Koma ganizirani zolakwa zanu chifukwa mwaphwanya malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ Anthu inu simunamvere mawu anga, koma munapitiriza kupanga njira zambirimbiri zopita kwa anthu achilendo+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira,”+ watero Yehova.’”

14 “Bwererani inu ana opanduka,”+ watero Yehova. “Ine ndakhala mwamuna wanu anthu inu.+ Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mu fuko lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+ 15 Ndidzakupatsani abusa amene mtima wanga wakonda+ ndipo iwo adzakuthandizani kudziwa zinthu zambiri ndiponso kumvetsa bwino zinthu.+ 16 Pamenepo mudzabalana ndi kuchuluka m’dzikoli masiku amenewo,” watero Yehova.+ “Iwo sadzafuulanso kuti, ‘Likasa la pangano la Yehova!’+ Sadzaliganiziranso m’mitima yawo, kulikumbukira,+ kapena kulilakalaka ndipo sadzapanganso likasa lina. 17 Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+

18 “M’masiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli,+ ndipo onse+ adzatuluka m’dziko la kumpoto ndi kulowa m’dziko limene ndinapereka kwa makolo anu monga cholowa chawo.+ 19 Ine ndanena kuti, ‘Mokondwera ndinakuikani pakati pa ana anga ndi kukupatsani dziko labwino,+ cholowa chimene mitundu yambiri ya anthu imachisirira!’ Ndipo ndinanenanso kuti, ‘Anthu inu mudzandiitana kuti, “Atate wanga!”+ ndipo mudzandilondola osabwerera.’ 20 ‘Ndithudi, monga mmene mkazi amasiyira mwamuna wake+ mwachinyengo, inunso a m’nyumba ya Isiraeli mwandichitira zachinyengo,’+ watero Yehova.”

21 Panjira zodutsidwadutsidwa pamveka mawu a ana a Isiraeli, kulira ndi kuchonderera kwawo. Pakuti iwo akhotetsa njira zawo+ ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+

22 “Bwererani, inu ana opanduka.+ Ndidzachiritsa kusakhulupirika kwanu.”+

“Ife tabwerera! Tabwera kwa inu, pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ 23 Ndithudi, zitunda ndi chipwirikiti chimene chimachitika m’mapiri+ ndiko kupembedza kwachinyengo.+ Kunena zoona chipulumutso cha Isiraeli chili mwa Yehova Mulungu wathu.+ 24 Chinthu chochititsa manyazi+ chadya ntchito yolemetsa ya manja a makolo athu kuyambira tili anyamata. Chadya nkhosa zawo, ng’ombe zawo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. 25 Tagona pansi mwamanyazi+ ndipo manyazi athuwo akupitiriza kutiphimba.+ Zimenezi zakhala choncho chifukwa chakuti ifeyo ndi makolo athu, tachimwira Yehova Mulungu wathu+ ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu+ kuyambira tili anyamata mpaka lero.”+

4 Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli, ubwerere kwa ine.+ Ndipo ngati ungachotse zinthu zako zonyansazo chifukwa cha ine,+ sudzakhalanso wothawathawa. 2 Ndipo ngati udzalumbira+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wachoonadi+ ndi chilungamo,’+ pamenepo mitundu ya anthu idzapeza madalitso* kudzera mwa iye ndipo idzadzitama m’dzina lake.”+

3 Zimene Yehova wanena kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu ndi izi: “Limani minda panthaka yabwino, ndipo musabzale mbewu pakati pa minga.+ 4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+

5 Nenani zimenezi mu Yuda anthu inu, ndipo zilengezeni ngakhale mu Yerusalemu.+ Fuulani ndi kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa m’dziko lonse.+ Fuulani kuti: “Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu. 7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+ 8 Pachifukwa chimenechi valani ziguduli,* anthu inu.+ Dzigugudeni pachifuwa ndi kulira mofuula,+ chifukwa mkwiyo woyaka moto wa Yehova sunatichokere.+

9 Yehova wanena kuti: “Zidzachitika pa tsikulo kuti mfumu sidzalimba mtima,+ chimodzimodzinso akalonga ake. Ansembe adzagwidwa ndi mantha ndipo aneneri adzadabwa.”+

10 Pamenepo ndinanena kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa anthu awa+ ndiponso Yerusalemu mwa kunena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ koma lupanga lawabaya* mpaka mumtima.”

11 Pa nthawiyo adzauza anthu awa ndi Yerusalemu kuti: “M’njira zodutsidwadutsidwa za m’chipululu zopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga+ mukutuluka mphepo yotentha.+ Mphepo imeneyi si youluzira mankhusu* kapena yoyeretsera tirigu. 12 Mphepo yamphamvu ikuchokera m’njirazo kubwera kwa ine. Ine ndidzawauza ziweruzo zanga.+ 13 Taonani! Mdani adzabwera ngati mitambo yamvula ndipo magaleta* ake ali ngati mphepo yamkuntho.+ Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+ Tsoka ife chifukwa tafunkhidwa. 14 Tsuka mtima wako ndi kuchotsa zoipa zonse, iwe Yerusalemu, kuti upulumuke.+ Kodi maganizo ako oipawo udzakhala nawo mpaka liti?+ 15 Pakuti mawu akumveka kuchokera ku Dani+ ndipo akulengeza uthenga wopweteka kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu.+ 16 Nenani zimenezi anthu inu. Nenani zimenezi kwa anthu a mitundu ina. Lengezani zimene zidzagwera Yerusalemu.”

“Alonda akubwera kuchokera kudziko lakutali+ ndipo adzalengeza uthenga wa zimene zidzagwera mizinda ya Yuda. 17 Iwo akhala ngati alonda a kunja kwa mzinda ndipo azungulira Yerusalemu kumbali zonse+ kuti amuukire chifukwa chakuti wandipandukira,”+ watero Yehova. 18 “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+ Limeneli ndilo tsoka lako chifukwa zidzakhala zowawa. Zidzatero chifukwa kupanduka kwako kwalowerera mpaka mumtima.”

19 M’mimba mwanga ine, m’mimba mwanga! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.+ Mtima wanga ukuvutika.+ Sindingathe kukhala chete pakuti ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.+ 20 Alengeza za kuphwanya kosakaziratu pakuti dziko lonse lafunkhidwa.+ Mwadzidzidzi, mahema anga ndi nsalu za mahema angawo zafunkhidwa+ m’kanthawi kochepa. 21 Kodi ndiona chizindikirocho ndi kumva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kufikira liti?+ 22 Anthu anga ndi opusa.+ Iwo sanaganizire za ine.+ Iwo ndi ana opanda nzeru ndipo sazindikira kalikonse.+ Iwo ndi anzeru pa kuchita zoipa koma sadziwa kuchita zabwino.+

23 Ndinaliona dzikolo, ndipo linali lopanda kanthu ndi lachabechabe.+ Ndinayang’ana kumwamba ndipo sikunali kuwala.+ 24 Ndinaona mapiri ndipo anali kugwedezeka. Zitunda zonse zinali kunjenjemera.+ 25 Ndinayang’anitsitsa koma sindinaone munthu aliyense. Ndipo zolengedwa zonse zouluka zinali zitathawa.+ 26 Ndinayang’anitsitsa ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo. Mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+ Zimenezi zinachitika ndi dzanja la Yehova chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.

27 Yehova wanena kuti: “Dziko lonseli lidzakhala bwinja+ ndipo ndidzawafafaniza.+ 28 Pachifukwa chimenechi dziko lidzalira+ ndipo kumwamba kudzachita mdima.+ Izi zili choncho chifukwa ndanena, ndaganiza zimenezi mozama, sindinadziimbe mlandu ndipo sindisintha maganizo anga.+ 29 Chifukwa cha phokoso la asilikali okwera pamahatchi ndiponso oponya mivi ndi uta, mzinda wonse ukuthawa.+ Alowa paziyangoyango ndi kuthawira m’matanthwe.+ Mumzinda uliwonse anthu athawamo ndipo palibe munthu amene akukhalamo.”

30 Iwe unali kuvala zovala zamtengo wapatali,* unali kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide ndipo unali kudzikongoletsa m’maso mwako ndi utoto wakuda.+ Tsopano utani popeza wafunkhidwa? Unali kutaya nthawi ndi kudzikongoletsa.+ Amene anali kukukhumba tsopano akukukana ndipo akufunafuna moyo wako.+ 31 Ine ndamva mawu ngati a mkazi amene akumva ululu. Ndamva ngati kubuula kwa mkazi amene akubereka mwana wake woyamba,+ koma ndi mawu a mwana wamkazi wa Ziyoni amene akupuma movutikira. Iye akutambasula manja ake+ ndi kulira kuti: “Tsoka ine, chifukwa ndatopa ndi anthu amene akufuna kundipha!”+

5 Pitani mukayendeyende m’misewu ya mu Yerusalemu kuti mukaone, mukafufuze m’mabwalo ake ndi kudziwa ngati mungapezeke munthu,+ ngati muli aliyense wochita chilungamo,+ kapena aliyense wokhulupirika.+ Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu. 2 Ngakhale atalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo!” adzakhala akulumbira mwachinyengo.+

3 Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo* kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+ 4 Ine ndinati: “Ndithudi, amenewa ndi anthu onyozeka. Anachita zinthu mopusa, pakuti anakana njira ya Yehova. Anakana chilamulo cha Mulungu wawo.+ 5 Ndidzapita kwa akuluakulu ndi kulankhula nawo,+ pakuti mosakayikira aganizira njira ya Yehova ndi chilamulo cha Mulungu wawo.+ Ndithudi onsewo athyola goli la Mulungu ndipo mosakayikira adula zomangira za Mulungu.”+

6 N’chifukwa chake mkango wa m’nkhalango wawaukira, mmbulu wa m’chipululu ukupitirizabe kuwawononga+ ndipo kambuku* akukhalabe tcheru pa mizinda yawo.+ Aliyense wotuluka m’mizindayo amakhadzulidwakhadzulidwa, chifukwa zolakwa zawo zachuluka ndipo zochita zawo za kusakhulupirika zawonjezeka kwambiri.+

7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu. 8 Iwo akhala ngati mahatchi amphongo achilakolako champhamvu chofuna kukwera, okhala ndi mavalo amphamvu. Aliyense amamemesa* mkazi wa mnzake.+

9 “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova.+ “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?”+

10 “Bwerani mudzaukire mizere yake ya mitengo ya mpesa ndi kuiwononga,+ koma anthu inu musaifafaniziretu.+ M’chotsereni mphukira zake zamasamba ambiri chifukwa si za Yehova.+ 11 Pakuti a m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda andichitiradi zachinyengo,” watero Yehova.+ 12 “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+ 13 Aneneri nawonso akulankhula zopanda pake ndipo mwa iwo mulibe mawu a Mulungu.+ Iwo adzakhala opanda pake ngati mawu awo omwewo.”

14 Chotero Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti: “Pakuti iwo akunena zimenezi, ndichititsa mawu anga m’kamwa mwako kukhala ngati moto+ koma anthu awa adzakhala ngati nkhuni ndipo motowo udzawanyeketsa.”+

15 “Tsopano anthu inu, ndikukubweretserani mtundu wa anthu akutali,+ inu a m’nyumba ya Isiraeli,” watero Yehova. “Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali,+ mtundu wakale, mtundu umene chilankhulo chawo simuchidziwa ndipo simungamve ndi kuzindikira zimene akulankhula. 16 Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka. Onse ndi amuna amphamvu.+ 17 Iwo adzadya zokolola zanu ndi mkate wanu.+ Amuna amenewo adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi. Adzadya nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu. Adzadya mtengo wanu wa mpesa ndi mtengo wanu wa mkuyu.+ Iwo adzagwetsa ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.”

18 Yehova wanena kuti: “Ngakhale masiku amenewo sindidzakufafanizani nonse anthu inu.+ 19 Ndiyeno mudzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zonsezi?’+ Pamenepo ukawayankhe kuti, ‘Popeza mwandisiya ine Mulungu wanu ndipo mwapita kukatumikira mulungu wachilendo m’dziko lanu, mudzatumikiranso alendo m’dziko limene si lanu.’”+

20 Mukanene izi m’nyumba ya Yakobo ndi kuzilengeza mu Yuda kuti: 21 “Tsopano tamverani izi anthu opusa inu, anthu opanda nzeru mumtima mwanu,+ amene muli ndi maso koma simukuona,+ muli ndi makutu koma simukumva.+ 22 ‘Kodi simundiopa?’+ watero Yehova. ‘Kapena kodi simukumva ululu waukulu chifukwa cha ine?+ Ine ndinaika mchenga kukhala malire a nyanja, malire okhalapo mpaka kalekale amene nyanjayo singadutse. Ngakhale kuti mafunde amawinduka sangadutse malirewo ndipo ngakhale amachita phokoso sangawapitirire.+ 23 Koma anthu awa ali ndi mtima wouma ndi wopanduka. Achoka panjira yanga ndipo akuyenda m’njira yawo.+ 24 Mumtima mwawo sananene kuti: “Tsopano tiyeni tiope Yehova Mulungu wathu,+ amene amatigwetsera mvula. Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira pa nyengo yake,+ ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi milungu yoikidwiratu imene timakolola.”+ 25 Zolakwa zanu ndi zimene zachititsa kuti zinthu zimenezi zithe ndipo machimo anu akutsekerezerani zabwino.+

26 “‘Zili choncho, chifukwa pakati pa anthu anga papezeka anthu oipa.+ Iwo amawabisalira ndi kuwayang’anitsitsa ngati mmene wosaka mbalame amachitira.+ Awatchera msampha wowononga pakuti iwo amagwira anthu. 27 Nyumba zawo zadzaza chinyengo+ ngati mmene mbalame zimadzazira m’chikwere.* N’chifukwa chake iwo alemera ndipo apeza chuma chambiri.+ 28 Iwo anenepa+ ndipo matupi awo asalala. Achitanso zinthu zoipa zosawerengeka. Iwo sanaweruze mlandu wa munthu aliyense mwachilungamo,+ ngakhale mlandu wa mwana wamasiye,*+ pofuna kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Iwo sanachitire chilungamo munthu wosauka.’”

29 “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?+ 30 Chinthu chodabwitsa, chinthu choopsa, chafika m’dziko:+ 31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

6 Bisalani, inu ana a Benjamini, thawani pakati pa Yerusalemu. Ku Tekowa+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Ku Beti-hakeremu+ kwezani moto wa chizindikiro, chifukwa chiwonongeko chachikulu, tsoka, lasuzumira kuchokera kumpoto.+ 2 Ndithudi mwana wamkazi wa Ziyoni wafanana ndi mkazi wachisasati* wooneka bwino.+ 3 Abusa ndi magulu awo a ziweto anali kubwera kwa iye. Anamanga mahema awo momuzungulira kuti amuukire.+ Aliyense wa iwo anali kudyetsa ziweto zake pamalo ake.+ 4 Anakonzekera kumuthira nkhondo ndipo anati:+ “Nyamukani, tiyeni tipite dzuwa lili paliwombo!”+

“Tsoka ife chifukwa nthawi yatithera ndipo zithunzithunzi zikupitiriza kutalika!”

5 “Nyamukani, ndipo tiyeni tipite usiku kuti tikawononge nsanja zake zokhalamo anthu.”+

6 Pakuti Yehova wa makamu wanena kuti: “Dulani mitengo+ kuti tipangire Yerusalemu chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Yerusalemu ndi mzinda woyenera kuimbidwa mlandu.+ Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+ 7 Monga mmene chitsime chimasungira madzi ake ali ozizira, Yerusalemu wasunga zoipa zake ngati zinthu zabwino. Mkati mwake mumamveka zachiwawa ndi kufunkha.+ Nthawi zonse ndimaona matenda ndi miliri mumzindawo. 8 Iwe Yerusalemu, mvera chilango+ kuti ndisatembenuke ndi kukufulatira chifukwa chonyansidwa nawe,+ kuti ndisakusandutse bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+

9 Yehova wa makamu wanena kuti: “Mosalephera adani adzakunkha otsalira a Isiraeli ngati mmene amakunkhira mphesa.+ Kweza dzanja lako ngati munthu amene akuthyola mphesa panthambi za mtengo wa mpesa.”

10 “Kodi ndilankhule ndi ndani ndipo ndichenjeze ndani kuti amve? Taonani! Makutu awo sanawachite mdulidwe, moti sangamve.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo,+ ndipo sakukondwera nawo.+ 11 Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova. Ndatopa ndi kukhala chete.”+

“Tsanulira mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu+ ndipo nthawi yomweyo uutsanulirenso pa kagulu ka anyamata okondana. Mwamuna pamodzi ndi mkazi wake, munthu wachikulire pamodzi ndi munthu wokalamba, onsewo adzagwidwa.+ 12 Nyumba zawo, minda yawo ndi akazi awo, zonse pamodzi zidzaperekedwa kwa anthu ena.+ Pakuti ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga anthu okhala m’dzikoli,” watero Yehova.+

13 “Pakuti aliyense wa iwo, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+ 14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+ 15 Kodi iwo anachita manyazi chifukwa chochita zinthu zonyansazi?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sadziwa n’komwe kuchita manyazi.+ Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.+ Pamene ndidzakhala ndikuwaimba mlandu adzapunthwa,” watero Yehova.

16 Yehova wauza anthuwo kuti: “Imani chilili panjira anthu inu, kuti muone ndi kufunsa za njira zakale, kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino.+ Mukaipeza muyende mmenemo+ kuti mupeze mpumulo wa miyoyo yanu.”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitiyendamo.”+ 17 “Koma anthu inu ndinakuutsirani alonda+ ndipo ndinati, ‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitidzamvera.”+ 18 “Choncho tamverani, inu mitundu ya anthu, kuti mudziwe anthu inu, zimene zidzawachitikira. 19 Tamverani, inu okhala padziko lapansi! Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+ chifukwa cha maganizo awo,+ pakuti sanamvere mawu anga ndipo anapitirizabe kukana chilamulo changa.”+

20 “N’chifukwa chiyani mukundibweretsera lubani* wochokera ku Sheba+ ndi mabango onunkhira ochokera kudziko lakutali? Zimenezi zili ndi ntchito yanji kwa ine? Nsembe zanu zopsereza zathunthu sizikundisangalatsa,+ ndipo nsembe zina zonse zimene mukupereka sizikundikondweretsa.”+ 21 Choncho Yehova wanena kuti: “Tsopano ndikuikira anthu awa zinthu zopunthwitsa,+ ndipo onse pamodzi, abambo ndi ana, adzapunthwa pa zinthu zimenezi, munthu aliyense limodzi ndi mnzake adzatheratu.”+

22 Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. Pali mtundu wamphamvu umene udzadzutsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 23 Iwo adzagwira uta ndi nthungo.*+ Umenewu ndi mtundu wankhanza ndipo sudzachita chisoni. Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanja+ ndipo adzabwera pamahatchi.+ Mtunduwo wafola pokonzekera kumenya nawe nkhondo ngati mmene mwamuna wankhondo amachitira, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.”+

24 Ife tamva uthenga wa zimenezi. Manja athu angoti lendee!+ Tagwidwa ndi nkhawa ndipo tikumva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.+ 25 Musatuluke kupita kunja ndipo musayende m’njira pakuti kumeneko kuli lupanga la mdani. Zochititsa mantha zili paliponse.+ 26 Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, vala chiguduli*+ ndi kuvimvinizika m’phulusa.+ Lira ngati kuti ukulira maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo. Lira mowawidwa mtima+ chifukwa wofunkha adzatiukira modzidzimutsa.+

27 “Ndakusandutsa woyesa zitsulo pakati pa anthu anga. Ndakusandutsa wofufuza mosamala ndipo udzaonetsetsa ndi kufufuza njira zawo.+ 28 Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+ oyenda uku ndi uku ngati anthu amiseche.+ Iwo ali ngati mkuwa ndi chitsulo. Onsewo ndi anthu owononga.+ 29 Zipangizo zopemerera moto+ zatenthedwa ndi moto ndipo pamoto wawo pakutuluka mtovu.+ Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu, ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+ 30 Anthu adzawatcha, ‘siliva wokanidwa,’+ pakuti Yehova wawakana.”+

7 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Imirira pachipata cha nyumba ya Yehova, ndi kulengeza kuti,+ ‘Tamverani mawu a Yehova nonsenu okhala mu Yuda, amene mumalowa pazipata izi kuti mukagwadire Yehova. 3 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Konzani njira zanu ndiponso zochita zanu kuti zikhale zabwino, ndipo ndidzachititsa anthu inu kukhalabe m’dziko lino.+ 4 Musamakhulupirire mawu achinyengo+ ndi kunena kuti, ‘Nyumba izi ndizo kachisi wa Yehova, inde ndi kachisi wa Yehova, ndithudi ndi kachisi wa Yehova!’ 5 Ngati mungakonze njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino, mukamaweruza molungama pakati pa munthu ndi mnzake,+ 6 ngati simudzapondereza mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye,+ komanso ngati simudzakhetsa magazi a munthu wopanda mlandu m’dziko lino,+ ndiponso ngati simudzatsatira milungu ina, zimene zingakubweretsereni tsoka,+ 7 inenso ndidzachititsa kuti mukhalebe m’dziko lino, dziko limene ndinapatsa makolo anu, ndipo mudzakhalamo mpaka kalekale.”’”+

8 “Inu mukukhulupirira mawu achinyengo, koma simudzapezapo phindu lililonse.+ 9 Kodi mungamabe,+ kupha,+ kuchita chigololo,+ kulumbira monama,+ kufukiza nsembe zautsi kwa Baala+ ndi kutsatira milungu ina imene simunali kuidziwa,+ 10 kenako n’kubwera kudzaima pamaso panga m’nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa+ n’kumanena kuti, ‘Ndithudi tidzapulumutsidwa,’ ngakhale mukuchita zinthu zonyansa zonsezi? 11 Kodi nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa,+ mwayamba kuiona ngati phanga la achifwamba?+ Inetu ndaona zimene mukuchita,” watero Yehova.+

12 “‘Pitani ku Silo,+ kumalo kumene poyamba kunali dzina langa,+ ndipo mukaone zimene ndinachitira malowo chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisiraeli.+ 13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+ 14 ndidzachita zofanana ndi zimene ndinachita ku Silo.+ Ndidzachita zimenezi panyumba imene ikutchedwa ndi dzina langa,+ imene inu mukuidalira,+ ndiponso malo amene ndinapatsa inu ndi makolo anu. 15 Ine ndidzakuthamangitsani, kukuchotsani pamaso panga,+ ngati mmene ndinathamangitsira abale anu onse, mbadwa zonse za Efuraimu.’+

16 “Tsopano iwe usawapempherere anthu awa, kapena kuwalirira kwa ine mochonderera. Usawaperekere pemphero, kapena kuwapemphera mochonderera,+ chifukwa ine sindidzakumvetsera.+ 17 Kodi sukuona zimene akuchita m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu?+ 18 Ana aamuna akutola nkhuni, abambo akuyatsa moto ndipo akazi akukanda ufa kuti apange makeke okapereka nsembe kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Ndipo akuthira pansi nsembe zachakumwa+ kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.+ 19 ‘Kodi iwo akukhumudwitsa ine?’ watero Yehova.+ ‘Kodi iwo sakudzikhumudwitsa okha kuti achite manyazi pankhope zawo?’+ 20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zikutsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamtengo wakuthengo,+ ndi pachipatso chilichonse chochokera m’nthaka yawo, ndipo udzayaka moti sudzazimitsidwa.’+

21 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Wonjezerani nsembe zanu zopsereza zathunthuzo pansembe zanu zinazo ndipo muzidye nokha.+ 22 Chifukwatu makolo anu, pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo, sindinawauze kapena kuwalamula kuti azipereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.+ 23 Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga,+ ndipo ndidzakhala Mulungu wanu,+ inuyo mudzakhala anthu anga. Muziyenda m’njira+ imene ndidzakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+ 24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu,+ ndipo anapitiriza kuyenda mwa zofuna zawo, mwa kuuma kwa mtima wawo woipawo,+ mwakuti anali kuyenda mobwerera m’mbuyo osati mopita patsogolo,+ 25 kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka m’dziko la Iguputo kufikira lero.+ Ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse aneneri, tsiku ndi tsiku ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza.+ 26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+

27 “Ukawauze mawu onsewa,+ ngakhale kuti sadzakumvera. Ukawaitane ngakhale kuti sadzakuyankha.+ 28 Ukawauze kuti, ‘Uwu ndiwo mtundu umene anthu ake sanamvere mawu a Yehova Mulungu wawo,+ ndipo sanamvere chilango.*+ Palibe munthu wokhulupirika pakati pawo, ndipo satchulanso n’komwe za kukhulupirika.’+

29 “Meta tsitsi lako lalitalilo ndi kulitaya.+ Ukwere pamapiri opanda mitengo ndi kuimba nyimbo yoimba polira pamenepo,+ pakuti Yehova wakana+ ndi kusiya mbadwo wa anthu amene wawakwiyira.+ 30 ‘Pakuti ana a Yuda achita zinthu zoipa m’maso mwanga,’ watero Yehova. ‘Aika zinthu zawo zonyansa m’nyumba yotchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+ 31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+

32 “‘Chotero taonani! Masiku akubwera,’ watero Yehova, ‘pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti ndiponso chigwa cha mwana wa Hinomu, koma adzawatchula kuti chigwa chopherako anthu.+ Iwo adzaika anthu m’manda ku Tofeti mpaka sikudzakhala malo okwanira.+ 33 Mitembo ya anthu awa idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi cha zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+ 34 Pamenepo ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi+ m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pakuti dzikoli lidzakhala litawonongedwa.’”+

8 “Pa nthawi imeneyo,” watero Yehova, “anthu adzatulutsa m’manda mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu amene anali mu Yerusalemu.+ 2 Mafupawo adzawamwaza poyera ndipo dzuwa, mwezi, ndi makamu onse akumwamba zidzawala pa iwo. Zinthu zimenezi ndi zimene iwo anali kuzikonda, kuzitumikira, kuzitsatira,+ kuzipembedza, ndi kuziweramira.+ Mafupawo sadzasonkhanitsidwa pamodzi kapena kuikidwa m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+

3 “Onse otsala a banja loipali, kulikonse kumene ndidzawabalalitsira,+ adzaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala moyo,”+ watero Yehova wa makamu.

4 “Ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwo adzagwa osadzukanso?+ Kodi mmodzi akabwerera, winanso sangabwerere?+ 5 N’chifukwa chiyani anthu a mu Yerusalemu ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi? Iwo akupitiriza kuchita zachinyengo+ ndipo akana kubwerera.+ 6 Ine ndinali tcheru+ ndipo ndinali kuwamvetsera.+ Zimene iwo anali kunena sizinali zoona. Panalibe munthu wolapa zoipa zimene anachita,+ amene ananena kuti, ‘Kodi ndachitiranji zimenezi?’ Aliyense akubwerera kunjira imene anthu ambiri akuitsatira,+ ngati hatchi imene ikuthamangira kunkhondo. 7 Ngakhale dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.+ Ndipo njiwa,+ namzeze* ndi pumbwa,* iliyonse mwa mbalame zimenezi imadziwa nyengo yobwerera kumene yachokera. Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+

8 “‘Anthu inu munganene bwanji kuti: “Ndife anzeru, ndipo tili ndi chilamulo cha Yehova”?+ Ndithudi, zolembera zachinyengo+ za alembi zagwiritsidwa ntchito mwachinyengo. 9 Anthu anzeru achita manyazi.+ Achita mantha ndipo adzagwidwa. Taonani! Iwo akana mawu a Yehova. Kodi ali ndi nzeru yotani tsopano?+ 10 Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena, ndipo minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+ Pakuti kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu aliyense wa iwo akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+ 11 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa mwana wamkazi wa anthu anga ponena kuti: “Kuli mtendere! Kuli mtendere!” pamene kulibe mtendere.+ 12 Kodi iwo anachita manyazi chifukwa anachita zinthu zonyansa?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sanali kudziwa n’komwe kuchita manyazi.+

“‘Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa. Pa nthawi yowalanga+ adzapunthwa,’ watero Yehova.+

13 “‘Pokolola ndidzawafafaniza,’ watero Yehova.+ ‘Mumtengo wa mpesa simudzapezeka mphesa,+ mumtengo wa mkuyu simudzapezeka nkhuyu, ndipo masamba adzafota. Zinthu zimene ndimawapatsa zidzawadutsa.’”

14 “N’chifukwa chiyani tikungokhala? Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ kuti tikafere kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watiweruza kuti tife,+ ndipo akutipatsa madzi apoizoni kuti timwe+ chifukwa tachimwira Yehova. 15 Tinali kuyembekezera mtendere, koma panalibe chabwino chilichonse.+ Tinali kuyembekezera kuchiritsidwa, koma m’malomwake tinali kuona zinthu zochititsa mantha.+ 16 Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani.+ Dziko lonse layamba kugwedezeka chifukwa cha phokoso la kulira kwa mahatchi ake amphongo.+ Adani akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zokhala mmenemo, mzinda ndi onse okhala mmenemo.”

17 “Inetu ndikutumiza njoka pakati panu, njoka zapoizoni,+ zimene simungaziimbire nyimbo kuti muziseweretse,+ ndipo zidzakulumani ndithu,” watero Yehova.

18 Ndagwidwa ndi chisoni chosatha.+ Mtima wanga wadwala. 19 Pakumveka mawu olirira thandizo a mwana wamkazi wa anthu anga ali kudziko lakutali.+ Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni?+ Kapena kodi mfumu ya Yerusalemu mulibe mmenemo?”+

“N’chifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba, ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?”+

20 “Nthawi yokolola yadutsa, ndipo nyengo ya chilimwe yatha. Koma ife sitinapulumutsidwe!”+

21 Ndasweka mtima+ chifukwa cha kuwonongeka+ kwa mwana wamkazi wa anthu anga. Ndine wachisoni. Ndadabwa kwambiri.+ 22 Kodi mu Giliyadi+ mulibe mafuta a basamu? Kapena kodi mulibe wochiritsa mmenemo?+ N’chifukwa chiyani nanga mwana wamkazi wa anthu anga sakuchira?+

9 Ndikanakonda kuti m’mutu mwanga mukhale madzi ambiri ndiponso kuti maso anga akhale magwero a misozi.+ Pamenepo ndikanalira usana ndi usiku chifukwa cha anthu ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga.+

2 Ndikanakonda kukhala ndi malo a m’chipululu ogona anthu apaulendo.+ Pamenepo ndikanasiya anthu anga ndi kuwachokera, pakuti onsewo ndi achigololo,+ gulu la anthu ochita zachinyengo.+ 3 Iwo amakunga lilime lawo ngati uta kuti aponye chinyengo,+ koma iwo si okhulupirika m’dzikoli.

“Iwo anali kuchita zoipa motsatizanatsatizana ndipo anandinyalanyaza,”+ watero Yehova.

4 “Aliyense wa inu asamale ndi mnzake,+ ndipo musakhulupirire m’bale aliyense.+ Pakuti munthu aliyense amalanda malo a m’bale wake,+ ndipo munthu aliyense amakhala akuyendayenda kunenera mnzake miseche.+ 5 Aliyense amapusitsa mnzake+ ndipo salankhula choonadi ngakhale pang’ono. Aphunzitsa lilime lawo kulankhula chinyengo.+ Iwo adzitopetsa okha ndi kuchita zinthu zoipa.+

6 “Iwe wakhala pakati pa chinyengo.+ Chifukwa cha chinyengo chawo akana kundidziwa ine,”+ watero Yehova.

7 Choncho, Yehova wa makamu wanena kuti: “Inetu ndikuwasungunula ndipo ndiyenera kuwasanthula.+ Nanga mwana wamkazi wa anthu anga ndingamuchitirenso zotani?+ 8 Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”+

9 “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu woterewu?+ 10 Pakuti ndidzalirira mapiri mokweza ndi modandaula+ ndipo ndidzaimba nyimbo yoimba polira, pamene ndikulirira mabusa a m’chipululu. Ndidzalirira zimenezi chifukwa adzakhala atazitentha+ moti palibe munthu amene adzadutsamo. Anthu sadzamva kulira kwa ziweto+ m’mabusamo ndipo zolengedwa zouluka m’mlengalenga ngakhalenso nyama zidzakhala zitathawamo, zitachoka.+ 11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+

12 “Kodi wanzeru ndani kuti amvetse zimenezi, kapenanso ndani amene Yehova wamulankhula kuti anene zimenezi?+ N’chifukwa chiyani dzikoli lidzawonongedwa ndiponso kutenthedwa n’kukhala ngati chipululu chopanda munthu wodutsamo?”+

13 Ndiyeno Yehova anayankha kuti: “Chifukwa chakuti iwo asiya chilamulo changa chimene ndinawapatsa kuti chizikhala pamaso pawo, komanso chifukwa chakuti iwo sanamvere mawu anga ndi kuwatsatira,+ 14 koma iwo anapitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndi kutsatira mafano a Baala,+ zinthu zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo.+ 15 Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa,+ ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+ 16 Ndidzawamwaza pakati pa mitundu ya anthu imene iwo kapena makolo awo sanaidziwe.+ Ndidzawakantha ndi lupanga kufikira nditawafafaniza.’+

17 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chitani zinthu mozindikira anthu inu, ndipo itanani akazi oimba nyimbo zoimba polira kuti abwere.+ Tumizani anthu kuti akaitane akazi odziwa kulira maliro,+ 18 kuti abwere mofulumira ndi kudzatiimbira nyimbo zoimba polira. Maso athu atuluke misozi, madzi atuluke m’maso athu owala.+ 19 Pakuti ku Ziyoni kwamveka anthu akulira mofuula kuti:+ “Tafunkhidwa!+ Tachita manyazi kwambiri! Pakuti tasiya dziko lathu ndiponso chifukwa atigwetsera nyumba zathu.”+ 20 Koma tamverani mawu a Yehova akazi inu, ndipo mutchere khutu ku mawu otuluka m’kamwa mwake. Kenako muphunzitse ana anu aakazi kulira maliro+ ndipo mkazi aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yoimba polira.+ 21 Pakuti imfa yatilowera m’nyumba kudzera m’mawindo. Yalowa munsanja zathu zokhalamo kuti mumsewu musapezeke mwana aliyense ndiponso kuti anyamata asapezeke m’mabwalo a mzinda.’+

22 “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Mitembo ya anthu idzangoti mbwee panthaka ngati manyowa. Idzakhala ngati tirigu amene angomumweta kumene koma palibe munthu womusonkhanitsa pamodzi.”’”+

23 Yehova wanena kuti: “Munthu wanzeru asadzitamande chifukwa cha nzeru zake.+ Munthu wamphamvu asadzitamande chifukwa cha mphamvu zake.+ Munthu wachuma asadzitamande chifukwa cha chuma chake.”+

24 “Koma amene akudzitamanda adzitamande pa chifukwa chakuti, amamvetsa bwino+ njira zanga ndipo amandidziwa, kuti ine ndine Yehova,+ amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi.+ Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa,”+ watero Yehova.

25 Yehova wanena kuti, “Taona masiku akubwera ndipo ndidzaimba mlandu aliyense wodulidwa koma amene sanachite mdulidwe wa mtima wake.+ 26 Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+

10 Anthu inu, a m’nyumba ya Isiraeli, imvani zimene Yehova wanena zokutsutsani. 2 Yehova wanena kuti: “Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono,+ ndipo musamaope zizindikiro zakumwamba, chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+ 3 Miyambo ya anthu amenewa+ ndi yopanda pake, chifukwa mmisiri amagwetsa mtengo+ m’nkhalango ndi kusema fano pogwiritsa ntchito sompho.+ 4 Akatero amakongoletsa fanolo ndi siliva komanso golide.+ Kenako amatenga nyundo ndi kukhomerera mafanowo pansi ndi misomali kuti asagwe.+ 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+

6 Ndithudi palibe aliyense wofanana ndi inu Yehova.+ Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu ndi lalikulu ndi lamphamvu.+ 7 Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+ 8 Onse pamodzi ndi opanda nzeru ndiponso opusa.+ Mtengo umangowalimbikitsa kuchita zachabechabe.+ 9 Siliva wosulidwa kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.+ Zonsezi zimakonzedwa mwaluso, ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo. Mafanowo amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Nawonso angokhala ntchito ya amisiri aluso.+

10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+ 11 Mitunduyo mukaiuze izi anthu inu: “Milungu+ imene sinapange kumwamba ndi dziko lapansi+ ndi imene idzawonongedwe padziko lapansi, pansi pa thambo.” 12 Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake,+ amene mwanzeru zake+ anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.+ 13 Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo,+ ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake.+

14 Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+ 15 Iwo ndi achabechabe, ntchito yoyenera kutonzedwa.+ Mulungu akadzatembenukira kwa iwo, adzawawononga.+

16 Koma Mulungu wa Yakobo+ sali ngati mafanowa. Iye ndi amene anapanga china chilichonse.+ Isiraeli ndiye ndodo ya cholowa chake.+ Dzina la Mulunguyo ndi Yehova wa makamu.+

17 Iwe mkazi wokhala m’masautso,+ sonkhanitsa ndi kunyamula katundu wako.+ 18 Yehova wanena kuti: “Tsopano nditaya kutali anthu okhala padziko lapansi,+ ndipo ndiwachititsa kuvutika mtima kuti adziwe masautso awo.”+

19 Tsoka ine chifukwa cha kuwonongedwa kwanga!+ Chilonda changa cha mkwapulo chakhala chosachiritsika. Ndipo ndanena kuti: “Ndithudi amenewa ndi matenda anga ndipo ndidzakhalabe nawo.+ 20 Hema wanga wafunkhidwa, ndipo zingwe zanga zonse zomangira hemayo aziduladula.+ Ana anga aamuna achoka ndi kundisiya ndipo kulibenso.+ Komanso palibe wotambasula kapena kudzutsa hema wanga. 21 Abusa achita zinthu mopanda nzeru,+ ndipo sanayese n’komwe kufunafuna Yehova.+ N’chifukwa chake sanachite zinthu mozindikira, ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.”+

22 Tamvetserani nkhani imene yamveka! Kugunda kwakukulu kukumveka kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo kudzasandutsa mizinda ya Yuda kukhala mabwinja, malo obisalamo mimbulu.+

23 Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.+ 24 Ndikonzeni, inu Yehova. Koma mundikonze ndi chiweruzo chanu+ osati mutakwiya+ chifukwa mungandifafanize.+ 25 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu+ amene akunyalanyazani,+ ndi pa mafuko amene sakuitana padzina lanu.+ Pakuti iwo adya Yakobo.+ Amudya ndipo akupitirizabe kumuwononga.+ Malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+

11 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Imvani mawu a pangano langa, anthu inu!

“Anthu a ku Yuda komanso okhala mu Yerusalemu ukawauze+ mawu amenewa. 3 Ukanene kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Munthu aliyense wosamvera mawu a m’pangano limeneli ndi wotembereredwa.+ 4 Makolo anu ndinawalamula kumvera mawu amenewa pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo,+ pamene ndinali kuwatulutsa m’ng’anjo yachitsulo.+ Ndinawalamula kuti, ‘Muzimvera mawu anga, ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo onse amene ndakupatsani.+ Mukatero mudzakhaladi anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu,+ 5 kuti ndikwaniritse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu+ kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ monga mmene zilili lero.’”’”

Pamenepo ine ndinayankha kuti: “Zikhale momwemo,* inu Yehova.”

6 Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Lalikira mawu onsewa m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu+ kuti, ‘Anthu inu, imvani mawu a pangano langa, ndipo muchite zimene akunena.+ 7 Inetu ndinalangiza makolo anu pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo+ ndipo ndikupitiriza kutero. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwalangiza kuti: “Muzimvera mawu anga.”+ 8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ M’malomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse amene ndinanena m’pangano langa, amene ndinawalamula kuti awasunge, koma sanawasunge.’”

9 Yehova anandiuzanso kuti: “Zadziwika kuti anthu a mu Yuda komanso okhala mu Yerusalemu akukonza chiwembu chondipandukira.+ 10 Iwo abwerera ku zolakwa zimene makolo awo+ anachita kalekale. Makolowo anakana kumvera mawu anga, m’malomwake anayamba kutsatira milungu ina kuti aitumikire.+ A m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda aphwanya pangano langa limene ndinachita ndi makolo awo.+ 11 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndiwagwetsera tsoka+ limene sadzatha kulithawa.+ Iwo adzandiitana kuti ndiwathandize, koma sindidzawamvera.+ 12 Ndipo mizinda ya Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu adzapita kukapempha thandizo kwa milungu imene akuifukizira nsembe zautsi.+ Koma milungu imeneyo sidzawapulumutsa pa nthawi ya tsoka lawo.+ 13 Pakuti milungu yako, iwe Yuda,+ yafanana ndi mizinda yako kuchuluka kwake. Ndipo chinthu chochititsa manyazi+ mwachimangira maguwa ansembe, anthu inu. Mwachimangira maguwa ansembe ochuluka mofanana ndi misewu ya mu Yerusalemu. Mwamanga maguwa ansembe kuti muzifukizira Baala nsembe zautsi.’+

14 “Tsopano iwe, usawapempherere anthu awa, ndipo usawalirire kwa ine mochonderera. Usawaperekere pemphero,+ chifukwa ine sindidzamvetsera pamene iwo akundiitana chifukwa cha tsoka limene lawagwera.+

15 “Kodi anthu anga okondedwa akufuna chiyani m’nyumba yanga+ pamene ambiri a iwo akuchita zoipa zoterezi?+ Kodi nyama yopatulika imene amaipereka nsembe idzawapulumutsa tsoka lawo likadzafika?+ Kodi iwo adzakondwera pa nthawi imeneyo?+ 16 Yehova wakutchulani dzina+ lakuti, ‘Mtengo waukulu wa maolivi wa masamba ambiri obiriwira, wokongola, wobala zipatso komanso wooneka bwino.’ Koma pali phokoso lamphamvu ndipo mtengowo auyatsa moto, komanso adani athyola nthambi zake.+

17 “Yehova wa makamu, Wokubzalani,+ wanena kuti tsoka lidzakugwerani chifukwa cha zoipa zimene a m’nyumba ya Isiraeli+ ndi a m’nyumba ya Yuda achita ndi kundikhumudwitsa nazo pofukizira Baala nsembe zautsi.”+

18 Yehova wandidziwitsa. Pa nthawiyo, inu Mulungu, munandionetsa zochita zawo.+ 19 Ndipo ine ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo wokondedwa mwapadera, amene akupita kukaphedwa.+ Ine sindinadziwe kuti andikonzera ziwembu+ ndi kunena kuti: “Tiyeni tiwononge mtengowu pamodzi ndi zipatso zake. Tiyeni timuchotse m’dziko la anthu amoyo,+ kuti dzina lake lisakumbukikenso.” 20 Koma Yehova wa makamu amaweruza mwachilungamo.+ Amafufuza impso ndi mtima.+ Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango, pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+

21 Choncho Yehova wanena motsutsana ndi anthu a ku Anatoti+ amene akufuna moyo wako, ndipo akunena kuti: “Usanenere m’dzina la Yehova,+ ngati ukufuna kuti tisakuphe.” 22 Yehova wa makamu wanena kuti: “Tsopano ndikuwapatsa chilango. Anyamata adzafa ndi lupanga.+ Ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala yaikulu.+ 23 Ndipo sipadzapezeka wotsala pakati pawo, chifukwa ndidzadzetsa tsoka pa anthu a ku Anatoti,+ m’chaka chimene ndidzawapatsa chilango.”+

12 Inu Yehova, ndinu Mulungu wolungama.+ Ndikabweretsa dandaulo kwa inu, ndipo ndikalankhula za chiweruzo chanu, mumachita chilungamo. Koma n’chifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino?+ N’chifukwa chiyani onse ochita chinyengo amakhala opanda nkhawa iliyonse? 2 Munawabzala ndipo iwo anazika mizu. Akupitirizabe kukula ndi kubala zipatso. Amakutchulani pafupipafupi, koma impso zawo zili kutali kwambiri ndi inu.+ 3 Inu Yehova, mumandidziwa bwino.+ Mumandiona ndipo mumasanthula mtima wanga kuti muone ngati uli wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,+ ndipo aikeni padera kuyembekezera tsiku lokaphedwa. 4 Kodi dzikoli lifotabe mpaka liti?+ Kodi zomera za m’minda yonse ziumabe mpaka liti?+ Chifukwa chakuti anthu a m’dzikoli ndi oipa, zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka zinachoka.+ Pakuti anthuwo akuti: “Iye sakuona zimene zidzatichitikira m’tsogolo.”

5 Pakuti unali kuthamanga ndi anthu oyenda pansi ndipo anali kukutopetsa, ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?+ Kodi ukumva kukhala wotetezeka m’dziko lamtendere?+ Ndiye udzatani ukadzakhala m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano?+ 6 Abale ako komanso anthu a m’nyumba ya bambo ako akuchitira chinyengo,+ ndipo mofuula akukunenera zinthu zoipa ali kumbuyo kwako. Usawakhulupirire m’pang’ono pomwe, ngakhale kuti akukuuza mawu abwino.+

7 “Ndasiya nyumba yanga.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka m’manja mwa adani ake.+ 8 Wokondedwa wangayo, amene ndi cholowa changa, wakhala ngati mkango kwa ine m’nkhalango ndipo wandibangulira. N’chifukwa chake ndadana naye.+ 9 Cholowa changa+ chili ngati mbalame yanthenga zamitundumitundu, yodya nyama. Mbalame zodya nyama zaizungulira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zam’tchire. Bwerani ndi anzanu kuti mudzaidye.+ 10 Abusa ambiri+ awononga munda wanga wa mpesa.+ Apondaponda cholowa changa.+ Cholowa changa chosiririka+ achisandutsa bwinja moti palibe aliyense amene akukhalamo. 11 Cholowa changacho achisandutsa bwinja+ moti chafota ndipo chawonongeka.+ Dziko lonse lakhala bwinja ndipo palibe aliyense amene zikumukhudza.+ 12 Anthu ofunkha adutsa m’njira zonse zodutsidwadutsidwa za m’chipululu. Lupanga la Yehova likuwononga anthu kuchokera kumalekezero a dziko kukafika kumalekezero ena a dziko.+ Palibe mtendere kwa munthu aliyense. 13 Afesa tirigu koma akolola minga.+ Agwira ntchito mpaka kudwala nayo, koma osapeza phindu lililonse.+ Iwo adzachita manyazi ndi zokolola zawo chifukwa mkwiyo waukulu wa Yehova udzawayakira.”

14 Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo + amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula pamalo awo.+ Ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo.+ 15 Ndiyeno ndikadzawazula ndidzawachitiranso chifundo+ moti ndidzawabwezeretsa. Ndidzabwezeretsa aliyense pacholowa chake, ndiponso pamalo ake.”+

16 “Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzaphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira m’dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ monga mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira m’dzina la Baala,+ anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga.+ 17 Koma akadzapanda kumvera, ine ndidzazula anthu a mitundu imeneyo. Ndidzawazula ndi kuwawononga,”+ watero Yehova.

13 Yehova wandiuza kuti: “Pita ukatenge lamba wansalu ndipo ukamumange m’chiuno mwako, koma asakakhudze madzi.” 2 Choncho ndinapita kukatenga lambayo mogwirizana ndi mawu a Yehova ndipo ndinamumanga m’chiuno mwanga. 3 Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kachiwiri kuti: 4 “Tenga lamba wabweretsayo amene wamumanga m’chiuno ndipo upite kumtsinje wa Firate.+ Kumeneko ukabise lambayo mumng’alu wa m’phanga.” 5 Pamenepo ndinanyamuka ndi kukabisa lambayo pafupi ndi mtsinje wa Firate monga mmene Yehova anandilamulira.

6 Ndiyeno patapita masiku ambiri Yehova anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kumtsinje wa Firate ndipo ukatenge lamba amene ndinakulamula kuti ukabise kumeneko.” 7 Choncho ndinapita kumtsinje wa Firate ndipo ndinakumba pamalo amene ndinabisapo lambayo ndi kumutenga. Koma nditamuona, anali atawonongeka moti sakanagwiranso ntchito iliyonse.

8 Pamenepo Yehova anandiuzanso kuti: 9 “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi lamba ameneyu, ndidzawononga kunyada kwa Yuda+ ndiponso kunyada kwakukulu kwa Yerusalemu. 10 Anthu oipa amenewa akukana kumvera mawu anga.+ Iwo akupitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina kuti aitumikire ndi kuigwadira.+ Anthu amenewa adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’ 11 ‘Ine ndinachititsa nyumba yonse ya Isiraeli ndi nyumba yonse ya Yuda kundimamatira+ mofanana ndi mmene lamba amagwirira m’chiuno mwa munthu,’ watero Yehova. ‘Ndinachita zimenezi kuti iwo akhale anthu anga,+ akhale dzina langa lotchuka,+ anditamande ndi kukhala chinthu changa chokongola. Koma iwo sanandimvere.’+

12 “Tsopano uwauze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo.”’+ Ukakawauza zimenezi, iwo adzakufunsa kuti, ‘Kodi ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo?’ 13 Pamenepo ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikuledzeretsa+ anthu onse a m’dzikoli, mafumu amene akukhala pampando wa Davide,+ ansembe, aneneri ndi onse okhala mu Yerusalemu. 14 Ndipo ndidzawombanitsa munthu ndi mnzake, abambo ndi ana awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Sindidzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni. Ndithu sindidzakhala ndi chifundo choti ndisawawononge.”’+

15 “Tamverani anthu inu. Tcherani khutu. Musadzikweze+ pakuti Yehova ndi amene wanena zimenezi.+ 16 Patsani Yehova Mulungu wanu ulemerero+ asanachititse mdima,+ komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa.+ Mudzayembekeza kuwala+ koma iye adzabweretsa mdima,+ ndipo adzachititsa mdima wandiweyani.+ 17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.

18 “Uza mfumu ndi mayi a mfumu+ kuti, ‘Khalani pamalo apansi,+ pakuti chisoti chanu chaulemerero chidzachotsedwa pamutu panu ndi kuikidwa pansi.’+ 19 Mizinda ya kum’mwera yatsekedwa moti palibe amene akuitsegula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo. Watengedwa wathunthu kupita ku ukapolo.+

20 “Kweza maso ako kuti uone anthu amene akubwera kuchokera kumpoto.+ Kodi nkhosa zimene anakupatsa, nkhosa zako zokongolazo zili kuti?+ 21 Kodi udzanenanji wina akadzatembenukira kwa iwe+ ngakhale kuti iweyo unamuchititsa kukhala bwenzi lako lapamtima, limene unali kukondana nalo kwambiri kuyambira pa chiyambi?+ Kodi zowawa za pobereka ngati za mkazi amene akubereka mwana sizidzakugwira?+ 22 Ukadzanena mumtima mwako kuti,+ ‘N’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+ pamenepo udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako+ ndipo zidendene zako zazunzidwa chifukwa zolakwa zako zachuluka.

23 “Kodi Mkusi*+ angasinthe khungu lake, kapena kodi kambuku angasinthe mawanga ake?+ Ngati angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti inunso amene munaphunzitsidwa kuchita zinthu zoipa mungathe kuchita zinthu zabwino.+ 24 Choncho ndidzakumwazani+ ngati mapesi amene akuuluka ndi mphepo kuchokera m’chipululu.+ 25 Limeneli ndilo gawo lako, malo ako amene ndakuyezera,”+ watero Yehova, “chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukupitirizabe kukhulupirira zinthu zachinyengo.+ 26 Ndidzakuvula siketi yako ndi kukuphimba nayo kumaso, moti udzachita manyazi.+ 27 Chigololo chako,+ kumemesa* kwako,+ khalidwe lako lotayirira la uhule, zonsezi zidzaonekera. Ndaona zinthu zako zonyansa pamapiri kuthengo.+ Tsoka kwa iwe Yerusalemu! Sungakhale woyera.+ Kodi udzakhalabe wosayera kufikira liti?”+

14 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala+ ndi awa: 2 Yuda akulira maliro+ ndipo zipata zake zagwetsedwa.+ Zagwetsedwa pansi+ ndipo kulira kwa Yerusalemu kwamveka kumwamba.+ 3 Anthu otchuka atuma anthu wamba kukatunga madzi.+ Anthu wambawo afika kuzitsime koma sanapeze madzi.+ Abwerera ndi ziwiya zopanda kanthu. Achita manyazi+ ndipo akhumudwa moti aphimba mitu yawo.+ 4 Alimi achita manyazi moti aphimba mitu yawo chifukwa chakuti m’dzikomo simunagwe mvula+ ndipo nthaka yawonongeka.+ 5 Mbawala yaikazi yabereka mwana mthengo, koma yamusiya chifukwa kulibe msipu. 6 Mbidzi+ zangoima chilili m’mapiri opanda kanthu. Zikupuma mwawefuwefu ngati mimbulu. Maso awo achita mdima chifukwa kulibe msipu.+ 7 Ngakhale kuti zolakwa zathu n’zoonekeratu, inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu,+ pakuti zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika zachuluka+ ndipo takuchimwirani.+

8 Inu chiyembekezo cha Isiraeli,+ Mpulumutsi wake+ pa nthawi ya nsautso,+ n’chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo m’dzikoli? N’chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wapaulendo amene wapatuka kuti agone usiku umodzi wokha?+ 9 N’chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru ndiponso ngati munthu wamphamvu amene sangathe kupulumutsa anthu ake?+ Komatu inu Yehova muli pakati pathu,+ ndipo ife tatchedwa ndi dzina lanu.+ Musatisiye.

10 Ponena za anthu awa Yehova wati: “Iwo akukonda kuyendayenda+ ndipo sanalamulire mapazi awo.+ Choncho Yehova sakukondwera nawo,+ moti adzakumbukira zolakwa zawo ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.”+

11 Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Usapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.+ 12 Pamene akusala kudya ine sindikumvetsera kuchonderera kwawo.+ Pamene akupereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zambewu ine sindikukondwera nazo,+ ndipo ndiwawononga ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.”+

13 Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+

14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, maula, mawu opanda pake+ ndi chinyengo cha mumtima mwawo.+ 15 Choncho Yehova wanena kuti: ‘Kunena za aneneriwo amene akulosera m’dzina langa ngakhale kuti sindinawatume, amenenso akunena kuti lupanga kapena njala sizidzafika m’dziko lino, ndidzawawononga ndi lupanga ndiponso njala.+ 16 Anthu amene akuwauza maulosi awowo, mitembo yawo idzatayidwa m’misewu ya Yerusalemu chifukwa cha njala ndi lupanga. Sipadzakhala wowaika m’manda, iwowo, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi+ chifukwa ndidzawatsanulira tsoka pamutu pawo.’+

17 “Ndiyeno uwauze kuti, ‘Maso anga atulutse misozi usiku ndi usana ndipo asasiye kutulutsa misozi,+ pakuti pamveka kugunda kwakukulu ndipo namwali, mwana wamkazi wa anthu anga wawonongedwa.+ Iye wawonongedwa ndi chilonda chachikulu cha mkwapulo chosachiritsika.+ 18 Ndipo ndikapita kunja kwa mzinda, ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+ Komanso ndikalowa mkati mwa mzinda ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala.+ Aneneri ndi ansembe, onse ayenda njira zosiyanasiyana kupita kudziko limene sakulidziwa.’”+

19 Kodi Yuda mwamukaniratu,+ kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+ N’chifukwa chiyani mwatikantha popanda wotichiritsa?+ Anthu anali kuyembekezera mtendere, koma palibe chabwino chimene chachitika. Anali kuyembekezera nthawi yochiritsidwa, koma taonani, kukuchitika zoopsa zokhazokha.+ 20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuipa kwathu ndi kulakwa kwa makolo athu.+ Inde, takuchimwirani.+ 21 Koma chifukwa cha dzina lanu, musatisiye.+ Musanyazitse mpando wanu wachifumu waulemerero.+ Kumbukirani pangano lanu limene munachita ndi ife ndipo musaliphwanye.+ 22 Kodi pakati pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse+ limene lingagwetse mvula? Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?+ Kodi si inu Yehova Mulungu wathu+ amene mumachititsa zimenezi? Chiyembekezo chathu chili mwa inu chifukwa ndinu amene mumachititsa zonsezi.+

15 Yehova anandiuza kuti: “Ngakhale Mose+ ndi Samueli+ akanaima pamaso panga, anthu awa sindikanawakomera mtima.+ Ndikanawapitikitsa pamaso panga kuti achoke.+ 2 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Tichoke kupita kuti?’ ukayankhe kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Woyenera kufa ndi mliri afe ndi mliri! Woyenera kufa ndi lupanga afe ndi lupanga! Woyenera kufa ndi njala yaikulu afe ndi njala yaikulu!+ Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!”’+

3 “‘Ndidzawagwetsera masoka a mitundu inayi,’+ watero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga+ ndi zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga. 4 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho,+ chifukwa cha zimene Manase, mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+ 5 Ndani adzakusonyeza chifundo, iwe Yerusalemu? Ndani adzakumvera chisoni+ ndipo ndani adzapatuka ndi kufunsa za moyo wako?’

6 “‘Iwe wandisiya,’+ watero Yehova. ‘Ukundifulatira ndi kundichokera.+ Choncho nditambasula dzanja langa kuti ndikukanthe ndi kukuwononga.+ Ndatopa nako kukumvera chisoni.+ 7 Ndipeta anthu anga ngati mbewu kuzipata za m’dzikoli. Ndithu, ndiwauluza ndi chifoloko.+ Ndiwaphera ana awo+ ndipo ndiwononga anthu anga chifukwa sanasiye kuchita zinthu zoipa.+ 8 Akazi awo amasiye achuluka kwambiri pamaso panga kuposa mchenga wa kunyanja. Ndibweretsa wowononga kwa mayi ndi mnyamata, dzuwa lili paliwombo.+ Ndiwachititsa kugwidwa ndi mantha ndi kuwasokoneza mwadzidzidzi.+ 9 Mkazi amene wabereka ana 7 wafooka ndipo akupuma movutikira.+ Kwa iye dzuwa lalowa masanasana,+ ndipo lachita manyazi ndi kuthedwa nzeru. Anthu otsala ndidzawapereka kwa adani awo kuti aphedwe ndi lupanga,’+ watero Yehova.”

10 Tsoka ine,+ chifukwa inu mayi anga munabereka ine munthu amene nthawi zonse ndimakangana ndipo ndimalimbana ndi dziko lonse.+ Sindinapereke ngongole komanso sanandikongoze kalikonse, koma anthu onse akunditemberera.+

11 Yehova wanena kuti: “Ndithu, ndidzakuchitira zinthu zabwino+ ndipo ndidzakuthandiza kuti ndikupulumutse kwa adani ako pa nthawi ya tsoka+ ndi nthawi ya nsautso.+ 12 Kodi munthu angathe kuthyolathyola chitsulo, chitsulo cha kumpoto? Ndiponso kodi angathe kuthyolathyola mkuwa? 13 Ndidzapereka chuma chanu anthu inu ndi zinthu zanu zamtengo wapatali kwa wofunkha+ popanda malipiro. Ndidzatero chifukwa cha machimo anu onse amene munachita m’dziko lanu lonse.+ 14 Ndidzachititsa adani anu kutenga chumacho ndi kupita nacho kudziko limene simukulidziwa,+ pakuti mkwiyo wanga wayatsa moto.+ Ndithu, moto wakuyakirani anthu inu.”

15 Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga.+ Ndikumbukireni+ ndipo mutembenuke ndi kundiyang’ana kuti mubwezere anthu ondizunza.+ Musandichotsere moyo wanga chifukwa chakuti simupsa mtima mwamsanga.+ Onani chitonzo chimene chili pa ine chifukwa cha dzina lanu.+ 16 Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya.+ Mawu anu amandikondweretsa+ ndi kusangalatsa mtima wanga,+ pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu,+ inu Yehova Mulungu wa makamu.+ 17 Sindinakhale pansi ndi gulu la anthu okonda kuchita nthabwala+ ndi kuyamba kusangalala nawo.+ Ndakhala pansi ndekhandekha chifukwa dzanja lanu lili pa ine,+ chifukwa mwandidzaza ndi mkwiyo.+ 18 N’chifukwa chiyani zopweteka zanga sizikutha+ ndiponso chilonda changa cha mkwapulo sichikupola?+ Chilondacho sichikumva mankhwala. Inu Mulungu, mwakhala ngati kasupe wosachedwa kuuma,+ ndiponso ngati mtsinje wosadalirika.+

19 Chotero Yehova wanena kuti: “Ukabwerera kwa ine, inenso ndidzakukonda,+ ndipo udzanditumikira.+ Ukasiyanitsa zinthu zamtengo wapatali ndi zinthu zopanda phindu, udzakhala ngati kamwa langa. Anthuwo adzabwera kwa iwe, koma iwe sudzapita kwa iwo.”

20 “Ndakuchititsa kukhala ngati mpanda wamkuwa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+ Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzakugonjetsa,+ pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa,”+ watero Yehova. 21 “Ndidzakulanditsa m’manja mwa anthu oipa+ ndipo ndidzakuwombola m’manja mwa anthu ankhanza.”

16 Ndiyeno Yehova anapitiriza kundiuza kuti: 2 “Usakwatire ndipo usakhale ndi ana aamuna kapena ana aakazi m’malo ano.+ 3 Ponena za ana aamuna ndi ana aakazi amene adzabadwa m’malo ano, komanso amayi ndi abambo obereka anawo m’dzikoli, Yehova wanena kuti,+ 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+

5 “Yehova wanena kuti, ‘Usalowe m’nyumba imene olira maliro akuchitiramo phwando, ndipo usapite kukalira nawo maliro kapena kuwamvera chisoni.’+

“‘Pakuti anthu awa ndawachotsera mtendere wanga, kukoma mtima kosatha ndi chifundo,’+ watero Yehova. 6 ‘Anthu onse a m’dzikoli, osasiyapo aliyense, adzafa ndithu. Sadzaikidwa m’manda+ ndipo anthu sadzadziguguda pachifuwa chifukwa cha iwo. Palibe aliyense amene adzadzichekacheka+ kapena kumeta mpala chifukwa cha iwo.+ 7 Ofedwa sadzapatsidwa chakudya chowatonthoza+ ndipo sadzapatsidwa zakumwa kuti awatonthoze pamaliro a bambo awo kapena mayi awo.+ 8 Ndipo usadzalowe m’nyumba yaphwando ndi kukhala nawo pansi kuti udye ndi kumwa.’+

9 “Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘M’masiku anu ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi m’malo ano, inu mukuona.’+

10 “Ndiyeno ukadzauza anthu awa mawu onsewa, ndipo iwo akadzakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wanena kuti adzatigwetsera tsoka lalikulu limeneli? Kodi talakwa chiyani ndipo tamuchimwira chiyani Yehova Mulungu wathu?’+ 11 Pamenepo udzawayankhe kuti, ‘“N’chifukwa chakuti makolo anu anandisiya,”+ watero Yehova, “ndipo anapitirizabe kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Koma ine anandisiya ndipo sanasunge malamulo anga.+ 12 Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa mtima+ wake woipawo ndipo simukundimvera.+ 13 Choncho ndidzakutayani kunja kukuchotsani m’dziko lino+ ndi kukupititsani kudziko limene inu ngakhalenso makolo anu sanalidziwe.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina+ usana ndi usiku chifukwa sindidzakumverani chifundo.”’

14 “‘Taonani! Masiku adzafika,’+ watero Yehova, ‘pamene sadzalumbiranso kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo!”+ 15 Koma adzalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene anawabalalitsira!” Ineyo ndidzawabwezeretsa kudziko lawo limene ndinapatsa makolo awo.’+

16 “‘Inetu ndikuitana asodzi ambiri,’ watero Yehova, ‘ndipo adzawawedza. Kenako ndidzaitana anthu ambiri osaka nyama,+ ndipo adzawasaka m’phiri lililonse, pachitunda chilichonse, ndi m’mapanga a m’matanthwe.+ 17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+ 18 Chotero ndisanawabwezeretse, ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse+ ndi machimo awo onse chifukwa choipitsa dziko langa.+ Anadzaza cholowa changa ndi mitembo ya zinthu zawo zochititsa mseru ndiponso zinthu zawo zonyansazo.’”+

19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga, malo anga achitetezo ndi malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.+ Mitundu ya anthu idzabwera kwa inu kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndipo idzati: “Ndithudi makolo athu analandira mafano* monga cholowa chawo.+ Analandira zinthu zachabechabe ndi zinthu zosapindulitsa.”+ 20 Kodi munthu wochokera kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeniyeni.+

21 “Choncho ine ndiwaphunzitsa. Pa nthawi ino yokha ndiwaonetsa dzanja langa ndi mphamvu zanga,+ ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”+

17 “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.+ Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi m’mitima+ yawo ndi panyanga za guwa lansembe.+ 2 Ngakhale ana awo aamuna akumbukira maguwa awo ansembe ndi mizati yawo yopatulika imene ili pansi pa mtengo waukulu wamasamba ambiri obiriwira, pamwamba pa zitunda zazitali+ 3 ndi pamapiri. Katundu wanu ndi chuma chanu chonse ndidzazipereka kuti anthu azifunkhe.+ Ndidzapereka malo anu okwezeka chifukwa cha tchimo limene lachitika m’madera anu onse.+ 4 Mwa kufuna kwanu munataya cholowa chimene ndinakupatsani.+ Inenso ndidzakuchititsani kutumikira adani anu m’dziko limene simunalidziwe.+ Anthu inu, ndakuyatsani ndi mkwiyo wanga+ ndipo moto wake udzayakabe mpaka kalekale.”

5 Yehova wanena kuti: “Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+ Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu,+ komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.+ 6 Adzakhala ngati mtengo umene uli pawokhawokha m’chipululu ndipo zabwino zikadzafika sadzatha kuziona.+ Iye adzakhala m’malo ouma a m’chipululu m’dziko la nthaka yamchere, kumene sikukhala anthu.+ 7 Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova.+ 8 Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira.+ Pa nthawi ya chilala+ sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.

9 “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+ Ndani angaudziwe? 10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+ 11 Munthu wopeza chuma mopanda chilungamo+ ali ngati nkhwali imene yasonkhanitsa mazira amene sinaikire. Chuma chakecho adzachisiya asanakwanitse ngakhale hafu ya zaka za moyo wake,+ ndipo pamapeto pake adzaonekera kuti ndi wopusa.”+

12 Mpando waulemerero wa Mulungu ndi wokwezeka kuyambira pa chiyambi.+ Ndipo mpando umenewu ndiwo malo athu opatulika.+ 13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli,+ onse amene akukusiyani adzachita manyazi.+ Mayina a anthu onse okupandukirani+ adzalembedwa pafumbi chifukwa asiya Yehova magwero a madzi amoyo.+ 14 Ndichiritseni inu Yehova, ndipo ndidzachiradi.+ Ndipulumutseni ndipo ndidzapulumukadi,+ pakuti ine ndimatamanda inu.+

15 Taonani! Ena akunena kuti: “N’chifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe?+ Tsopanotu akwaniritsidwe.” 16 Koma ine sindinaleke kukutsatirani monga m’busa wanu. Ndipo sindinalakalake kuti tsiku loopsa lifike. Inu Mulungu, mukudziwa mawu otuluka pakamwa panga chifukwa ndinawalankhula pamaso panu. 17 Musakhale chinthu choopsa kwa ine.+ Inu ndinu pothawirapo panga pa tsiku la tsoka.+ 18 Anthu amene amandizunza achite manyazi+ koma musalole kuti ineyo ndichite manyazi.+ Anthuwo agwidwe ndi mantha aakulu koma musalole kuti ine ndigwidwe ndi mantha aakulu. Agwetsereni tsoka+ ndipo muwaphwanye kuwirikiza kawiri.+

19 Yehova wandiuza kuti: “Pita ukaime pachipata cha ana a anthu pamene mafumu a Yuda amalowera ndi kutulukira. Kenako ukaimenso pazipata zina zonse za Yerusalemu.+ 20 Ndipo ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu nonse okhala mu Yuda komanso inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumalowera pazipata izi.+ 21 Yehova wanena kuti: “Samalani moyo wanu.+ Katundu aliyense amene mukufuna kulowa naye pazipata za Yerusalemu musamunyamule pa tsiku la sabata.+ 22 Musatulutse katundu aliyense kuchokera m’nyumba zanu pa tsiku la sabata ndipo musamagwire ntchito iliyonse.+ Tsiku la sabata muziliona kukhala lopatulika monga mmene ndinalamulira makolo anu.+ 23 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu+ moti anapitiriza kuumitsa khosi+ lawo kuti asamve ndi kulandira mwambo.”’*+

24 “‘“Ndipo mukadzandimvera,”+ watero Yehova, “mwa kusalowa ndi katundu pazipata za mzindawu pa tsiku la sabata+ ndi kuona tsiku la sabata kukhala lopatulika mwa kusagwira ntchito iliyonse pa tsikuli,+ 25 pazipata za mzindawu padzalowa mafumu ndi akalonga+ okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mafumuwo pamodzi ndi akalonga awo adzalowa atakwera magaleta ndi mahatchi. Adzalowa pamodzi ndi anthu a mu Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndipo mumzindawu mudzakhala anthu mpaka kalekale. 26 Anthu adzabwera kuchokera m’mizinda ya Yuda, m’madera ozungulira Yerusalemu, m’dziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ m’dera lamapiri+ komanso kuchokera kum’mwera.*+ Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani*+ ndi nsembe zoyamikira.+

27 “‘“Koma ngati simudzamvera mawu anga akuti muziona tsiku la sabata kukhala lopatulika ndi kuti musamanyamule katundu+ kulowa naye pazipata za Yerusalemu pa tsiku la sabata, ine ndidzatentha ndi moto zipata za mzindawu.+ Motowo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Yerusalemu+ ndipo sudzazimitsidwa.”’”+

18 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Nyamuka, pita kunyumba ya woumba mbiya,+ ndipo ndikakuuza mawu anga kumeneko.”

3 Pamenepo ndinapita kunyumba ya woumba mbiya, ndipo ndinam’peza akugwira ntchito yake pamikombero ya woumba mbiya. 4 Chiwiya chimene anali kupanga ndi dongo chinawonongeka ndi dzanja la woumbayo. Choncho iye anasintha ndipo anapanga chiwiya china ndi dongo lomwelo malinga ndi zimene anaona kuti n’zabwino.+

5 Ndiyeno Yehova anapitiriza kundiuza kuti: 6 “‘Anthu inu, kodi sindingathe kukuchitirani mofanana ndi mmene woumba mbiyayu anachitira, inu nyumba ya Isiraeli?’ watero Yehova. ‘Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine, inu nyumba ya Isiraeli.+ 7 Pa nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndizula, kugwetsa ndi kuwononga mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu,+ 8 ndiyeno anthuwo n’kusiya zoipa zimene anali kuchita, zimene ndinawadzudzula nazo,+ pamenepo ndidzasintha maganizo anga kuti ndisawagwetsere tsoka limene ndinafuna kuwagwetsera.+ 9 Koma pa nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndimanga ndi kubzala mtundu wa anthu kapena ufumu,+ 10 ndiyeno anthuwo n’kumachita zoipa pamaso panga mwa kusamvera mawu anga,+ pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa zabwino zimene ndinali kufuna kudzawachitira pofuna kuwapindulitsa.’

11 “Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka, ndipo ndikuganizira zokuchitani chinthu choipa.+ Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.”’”+

12 Koma iwo anati: “Zimenezo ayi!+ Ife titsatira maganizo athu, ndipo aliyense wa ife adzaumitsabe mtima wake woipawo.”+

13 Choncho Yehova wanena kuti: “Funsafunsani pakati pa mitundu ya anthu. Ndani anamvapo zoterezi? Namwali wa Isiraeli wachita chinthu choopsa mopyola malire.+ 14 Kodi chipale chofewa chidzasungunuka ndi kuchoka pamapiri a ku Lebanoni? Kapena kodi madzi ochokera kudziko lina ozizira bwino, amene akudontha, adzauma? 15 Pakuti anthu anga andiiwala+ moti amapereka nsembe zautsi kwa chinthu chopanda pake,+ ndiponso amapunthwitsa anthu amene akuyenda panjira zawo,+ m’njira zakale,+ ndi kuwayendetsa m’njira zina, njira zokumbikakumbika. 16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chodabwitsa kwa ena,+ chinthu chimene adzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyang’anitsitsa modabwa ndipo adzapukusa mutu wake.+ 17 Ndidzawamwaza pamaso pa adani awo ngati mmene mphepo yochokera kum’mawa imamwazira fumbi.+ Sindidzawaonetsa nkhope yanga,+ koma ndidzawafulatira pa tsiku la tsoka lawo.”

18 Iwo anapitiriza kunena kuti: “Bwerani anthu inu, timukonzere chiwembu Yeremiya,+ pakuti chilamulo sichidzachoka pakamwa pa ansembe athu.+ Anthu athu anzeru sadzaleka kupereka malangizo ndiponso aneneri athu sadzaleka kulosera.+ Tabwerani, tiyeni timuukire ndi malilime athu+ ndipo tisamvere mawu ake ngakhale pang’ono.”

19 Ndimvereni, inu Yehova, ndipo imvani mawu a anthu amene akutsutsana nane.+ 20 Kodi zabwino amazibwezera ndi zoipa?+ Kumbukirani nthawi zonse zija pamene ndinaima pamaso panu kuwalankhulira zabwino kuti muwachotsere mkwiyo wanu.+ Koma iwo tsopano andikumbira mbuna.+ 21 Chotero ana awo muwakhaulitse ndi njala yaikulu,+ ndipo aphedwe ndi lupanga.+ Akazi awo akhale amasiye ndipo ana a akaziwo afe.+ Amuna awo afe ndi mliri woopsa ndipo anyamata awo aphedwe ndi lupanga pa nkhondo.+ 22 M’nyumba zawo mumveke kulira mukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi,+ chifukwa andikumbira mbuna kuti andigwire ndipo anditchera misampha kuti akole mapazi anga.+

23 Koma inu Yehova mukudziwa bwino chiwembu chimene andikonzera kuti andiphe.+ Musakhululukire* cholakwa chawo, ndipo musafafanize tchimo lawolo pamaso panu. Koma iwo apunthwe pamaso panu.+ Muwachitire zimenezi pa nthawi ya mkwiyo wanu.+

19 Yehova wanena kuti: “Pita, ukatenge botolo la mafuta ladothi kwa woumba mbiya+ ndipo ukaitane ena mwa atsogoleri a anthu ndi ena mwa akuluakulu a ansembe. 2 Ndiyeno ukapite kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ chimene chili pafupi ndi khomo la Chipata cha Mapale.* Kumeneko ukanene mawu onse amene ndikuuze.+ 3 Ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu.+ Yehova wa makamu,+ Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti:

“‘“Ine ndikubweretsa tsoka pamalo ano, ndipo aliyense akadzamva za tsoka limeneli, makutu ake adzalira.+ 4 Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+ 5 Iwo amangiranso Baala malo okwezeka kuti azitentherapo ana awo aamuna monga nsembe zopsereza zathunthu zoperekedwa kwa Baala.+ Ine sindinawalamule zimenezi kapena kuzitchula,+ ndipo sindinaziganizirepo mumtima mwanga.”’+

6 “‘Yehova wanena kuti: “Chotero taonani! Masiku akubwera pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti+ ndiponso chigwa cha mwana wa Hinomu,+ koma adzawatchula kuti chigwa chopherako anthu. 7 Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu m’malo ano,+ ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo.+ Mitembo yawo ndidzaipereka kwa zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+ 8 Ndidzasandutsa mzindawu kukhala chinthu chodabwitsa kwa ena, chimene azidzachiimbira mluzu.+ Aliyense wodutsa pafupi nawo adzauyang’anitsitsa modabwa ndipo adzaulizira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+ 9 Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikiza nazo.”’+

10 “Ukaswe botololo pamaso pa amuna amene akupita nawe. 11 Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ndidzaswa anthu awa ndi mzinda uwu ngati mmene munthu amaswera botolo lopangidwa ndi woumba mbiya moti sangathe kulikonzanso.+ Ndipo adzaika maliro ku Tofeti+ mpaka sipadzapezekanso malo oika maliro kumeneko.”’+

12 “‘Ndi mmene ndidzachitira ndi malo awa ndiponso ndi anthu onse okhala mmenemu. Mzinda uwu ndidzausandutsa kukhala ngati Tofeti,’+ watero Yehova. 13 ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake anali kufukizirapo nsembe zautsi kwa makamu akumwamba+ ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+

14 Ndiyeno Yeremiya anabwerako ku Tofeti+ kumene Yehova anamutuma kuti akalosere. Kenako anakaima m’bwalo la nyumba ya Yehova ndi kuuza anthu onse kuti:+ 15 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndikubweretsera mzinda uwu ndi mizinda yake yonse yozungulira masoka onse amene ndinanena, chifukwa anthu ake aumitsa khosi lawo kuti asamvere mawu anga.’”+

20 Tsopano Pasuri, mwana wa Imeri,+ wansembe, amenenso anali mtumiki wamkulu panyumba ya Yehova,+ anakhala tcheru kumvetsera pamene Yeremiya anali kulosera mwa kunena mawu amenewa. 2 Kenako Pasuri anamenya mneneri Yeremiya+ ndi kumuika m’matangadza+ amene anali pa Chipata Chakumtunda cha Benjamini, cha m’nyumba ya Yehova. 3 Ndiyeno pa tsiku lotsatira, Pasuri anamasula Yeremiya m’matangadzawo.+ Pamenepo Yeremiya anamuuza kuti:

“Yehova wanena kuti dzina lako+ silikhalanso Pasuri koma Chochititsa Mantha paliponse.+ 4 Pakuti Yehova wanena kuti, ‘Inetu ndikukusandutsa chinthu chochititsa mantha kwa iwe mwini ndi kwa anzako onse, ndipo adzaphedwa ndi lupanga la adani awo+ iwe ukuona.+ Anthu onse a mu Yuda ndidzawapereka m’manja mwa mfumu ya ku Babulo. Ena adzapita nawo ku Babulo ndipo ena adzawapha ndi lupanga.+ 5 Ndipo ndidzatenga zinthu zonse zosungidwa mumzindawu, katundu wawo yense, zinthu zonse zamtengo wapatali ndi chuma chonse cha mafumu a Yuda, n’kuzipereka m’manja mwa adani awo.+ Ndipo adaniwo adzafunkha zinthu zimenezi ndi kupita nazo ku Babulo.+ 6 Koma kunena za iwe Pasuri, ndi onse okhala m’nyumba yako, mudzapita ku ukapolo.+ Iwe udzapita ku Babulo ndipo udzafera kumeneko ndi kuikidwa m’manda komweko pamodzi ndi anzako onse,+ chifukwa walosera kwa iwo monama.’”+

7 Mwandidabwitsa inu Yehova, ndipo ndadabwa. Mwagwiritsa ntchito mphamvu zanu pa ine ndipo mwapambana.+ Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse. Aliyense akungondinyoza.+ 8 Nthawi zonse ndikalankhula mawu anu ndimalira. Ndimanena za chiwawa ndi kufunkhidwa,+ pakuti mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kutonzedwa tsiku lonse.+ 9 Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.”+ Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.+ 10 Pakuti ndinamva zoipa zimene ambiri anali kunena.+ Zinali zochititsa mantha paliponse. Iwo anali kunena kuti, “Fotokozani kuti ifenso tinene za iye.”+ Munthu aliyense anali kundiuza kuti “Mtendere!” koma anali kundiyang’anira kuti ndilakwitse chinachake+ ndipo anali kunena kuti: “Achita chinachake chopusa+ ameneyu ndipo timugonjetsa ndi kumubwezera.” 11 Koma Yehova anali nane+ ngati msilikali wamphamvu ndi woopsa.+ N’chifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.+ Adzachita manyazi kwambiri chifukwa adzaona kuti sizinawayendere bwino. Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+

12 Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama.+ Mumaona impso ndi mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+ pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+

13 Imbirani Yehova anthu inu! Tamandani Yehova! Pakuti walanditsa moyo wa munthu wosauka m’manja mwa anthu ochita zoipa.+

14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene mayi anga anandibereka lisadalitsike!+ 15 Atembereredwe munthu amene anabweretsa uthenga wabwino kwa bambo anga powauza kuti: “Mkazi wako wakuberekera mwana wamwamuna.” Munthuyo anawasangalatsa kwambiri bambo anga.+ 16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova waigonjetsa popanda kuimvera chisoni.+ M’mawa kwambiri azimva kulira kofuula ndipo masana azimva chizindikiro chochenjeza.+

17 N’chifukwa chiyani sanandiphe ndili m’mimba kuti mayi anga akhale manda anga, ndiponso kuti akhale ndi pakati mpaka kalekale?+ 18 N’chifukwa chiyani ndinabadwa?+ Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni,+ ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?+

21 Yehova anauza Yeremiya mawu,+ pamene Mfumu Zedekiya+ inatumiza Pasuri+ mwana wa Malikiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, ndi uthenga wakuti: 2 “Chonde tifunsire kwa Yehova+ chifukwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo akufuna kumenyana nafe nkhondo.+ Mwina Yehova adzatichitira imodzi mwa ntchito zake zamphamvu kuti Nebukadirezarayo atichokere.”+

3 Pamenepo Yeremiya anawauza kuti: “Mukauze Zedekiya kuti, 4 ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Anthu inu, ine ndichititsa zida zimene zili m’manja mwanu kukutembenukirani. Zimenezi ndi zida zimene mukugwiritsa ntchito pomenyana ndi mfumu ya Babulo+ ndi Akasidi+ amene azungulira kunja kwa mpanda wanu. Ndipo ndisonkhanitsa zida zanuzo pakati pa mzinda uwu.+ 5 Ndidzamenyana nanu+ ndi mkono wotambasula ndiponso dzanja lamphamvu. Ndidzachita zimenezi nditakwiya, nditapsa mtima, ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ 6 Ndidzapha onse okhala mumzinda uwu, anthu ndi nyama zomwe. Adzafa ndi mliri waukulu.”’+

7 “‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu onse, onse opulumuka ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu mumzinda uwu, ndidzawapereka m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo. Ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa amene akufuna moyo wawo. Nebukadirezara adzawapha ndi lupanga+ ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+

8 “Anthu awa uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu, ndikuika njira ya moyo ndi njira ya imfa pamaso panu.+ 9 Anthu amene adzakhalabe mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.+ Koma amene adzatuluka ndi kugwidwa ndi Akasidi amene akuzungulirani adzakhala ndi moyo. Iwo adzapulumutsa moyo wawo.”’+

10 “‘“Mzinda uwu ndaukana* ndipo ukumana ndi tsoka osati zabwino,”+ watero Yehova. “Ndidzaupereka m’manja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo idzautentha ndi moto.”+

11 “‘Anthu inu, imvani zimene Yehova wanena zokhudza banja la mfumu ya Yuda.+ 12 Inu a m’nyumba ya Davide,+ Yehova wanena kuti: “M’mawa uliwonse+ muziweruza mwachilungamo,+ ndipo muzilanditsa munthu kwa anthu achinyengo amene akufuna kumulanda katundu.+ Muzitero kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto+ ndi kukutenthani popanda wouzimitsa chifukwa cha kuipa kwa zochita zanu.”’+

13 “‘Ndakuukira iwe mkazi wokhala m’chigwa,+ iwe mzinda wapathanthwe limene lili pamalo athyathyathya,’ watero Yehova. ‘Koma inu amene mukunena kuti: “Ndani adzabwera kuno kuti atiukire? Ndipo ndani adzalowa m’nyumba zathu?”+ imvani izi, 14 ndidzakuimbani mlandu+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zanu,’+ watero Yehova. ‘Ndidzayatsanso moto m’nkhalango za mzindawu,+ moti udzanyeketsa zinthu zonse zouzungulira.’”+

22 Yehova wanena kuti: “Pita kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndipo kumeneko ukanene mawu awa. 2 Ukanene kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mfumu ya Yuda amene mwakhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mumve mawu amenewa inuyo, atumiki anu komanso anthu anu amene amalowa pazipata izi.+ 3 Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo, muzilanditsa munthu amene anthu achinyengo akufuna kumulanda katundu wake. Musachitire nkhanza mlendo aliyense wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye* kapena mkazi wamasiye.+ Musawachitire zachiwawa.+ Musakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa m’dziko lino.+ 4 Mukatsatiradi mawu amenewa, pazipata za nyumba iyi padzalowa mafumu okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mfumu iliyonse idzalowa pamodzi ndi atumiki ake ndi anthu ake atakwera magaleta ndi mahatchi.”’+

5 “‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pali ine mwini+ kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ watero Yehova.+

6 “Ponena za nyumba ya mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Kwa ine, iwe uli ngati Giliyadi ndiponso ngati nsonga ya phiri la ku Lebanoni.+ Ndithudi ndidzakusandutsa chipululu+ ndipo m’mizinda iyi simudzapezeka aliyense wokhalamo.+ 7 Ndidzakuutsira owononga+ ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi zida zake.+ Iwo adzadula mitengo yako yabwino kwambiri ya mkungudza+ ndi kuigwetsera pamoto.+ 8 Anthu a mitundu yambiri adzadutsa pafupi ndi mzinda uwu ndipo adzafunsana kuti: “N’chifukwa chiyani Yehova anachitira mzinda waukuluwu zinthu zoterezi?”+ 9 Ndipo adzanena kuti: “Anauchitira zimenezi chifukwa chakuti anthu a mumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo+ ndi kuyamba kulambira milungu ina ndi kuitumikira.”’+

10 “Munthu wakufa musamulire kapena kumumvera chisoni anthu inu.+ Lirani munthu amene watengedwa kupita ku ukapolo chifukwa sadzabwererakonso ndipo sadzaonanso dziko lakwawo. 11 Ponena za Salumu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene akulamulira m’malo mwa bambo ake Yosiya,+ amene anachoka m’dziko lino kupita ku ukapolo, Yehova wanena kuti, ‘Sadzabwereranso kwawo, 12 chifukwa akafera kudziko laukapolo kumene amutengera ndipo dziko lino sadzalionanso.’+

13 “Tsoka amene akumanga nyumba yake+ komanso zipinda zake zam’mwamba mopanda chilungamo mwa kugwiritsa ntchito anthu kwaulere, osawapatsa malipiro.+ 14 Iye akunena kuti, ‘Ndimanga nyumba yaikulu ndi zipinda zikuluzikulu zam’mwamba.+ Ndikulitsa mawindo ake ndipo ndiyala matabwa a mkungudza+ ndi kupaka utoto wofiira.’+ 15 Kodi upitiriza kulamulira chifukwa chakuti matabwa a mkungudzawa akukuchititsa kukhala wapamwamba kuposa ena? Kodi bambo ako sanali kudya, kumwa ndi kuchita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo?+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinawayendera bwino.+ 16 Anali kunenera mlandu anthu osautsika ndi osauka.+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinayenda bwino. ‘Kodi sanachite zimenezi chifukwa chakuti anali kundidziwa?’ watero Yehova. 17 ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’

18 “Choncho ponena za Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sadzamulira monga mmene anthu amachitira kuti: “Kalanga ine m’bale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!” Sadzamulira kuti: “Kalanga ine mbuye wanga! Kalanga ine, onani mmene ulemerero wake wathera!”+ 19 Adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.+ Adzamukoka kudutsa naye pazipata za Yerusalemu ndi kukamutaya kunja.’+

20 “Pita ku Lebanoni+ kuti ukalire kumeneko, ndipo ukafuule ku Basana.+ Ukalirenso ku Abarimu+ chifukwa amene anali kukukonda kwambiri agonjetsedwa.+ 21 Ndinalankhula nawe pamene unali pa ufulu,+ koma iwe unandiyankha kuti, ‘Sindidzamvera.’+ Wakhala ukuchita zimenezi kuyambira uli wachinyamata, moti sunamvere mawu anga.+ 22 Mphepo idzaweta abusa ako onse+ ndipo anthu onse amene akukukonda kwambiri adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Pa nthawi imeneyo udzachita manyazi ndipo udzanyazitsidwadi chifukwa cha tsoka limene lidzakugwere.+ 23 Inu okhala mu Lebanoni,+ amene mukuwetedwa m’nyumba zamitengo ya mkungudza,+ mudzausadi moyo zowawa za pobereka zikadzakugwerani,+ mukadzamva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.”+

24 “‘Pali ine, Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, ‘ngakhale iwe Koniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, utakhala mphete yodindira+ kudzanja langa lamanja, ndidzakuvula!+ 25 Ndipo ndidzakupereka m’manja mwa anthu ofunafuna moyo wako,+ m’manja mwa amene umawaopa, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ndiponso m’manja mwa Akasidi.+ 26 Iwe ndi mayi ako+ amene anakubereka, ndidzakuponyani kudziko lina limene anthu inu simunabadwireko ndipo mudzafera kumeneko.+ 27 Ndidzakuponyani kudziko limene mitima yanu idzalakalaka kubwererako, koma simudzabwererako.+ 28 Kodi munthu uyu Koniya+ wangokhala chiwiya chonyozeka, chophwanyika+ komanso chosasangalatsa?+ N’chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuyenera kugwetsedwa ndi kuponyedwa kudziko limene sakulidziwa?’+

29 “Iwe dziko lapansi, dziko lapansi, dziko lapansi, tamvera mawu a Yehova.+ 30 Yehova wanena kuti, ‘Lembani kuti munthu uyu alibe ana,+ munthu wamphamvu amene zinthu sizidzamuyendera bwino m’masiku a moyo wake. Pakuti mwa ana ake onse, palibe ndi mmodzi yemwe amene zinthu zidzamuyendera bwino.+ Palibe ngakhale mmodzi amene adzakhala pampando wachifumu wa Davide+ ndi kulamulira mu Yuda.’”

23 “Tsoka abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pamalo anga odyetsera ziweto!”+ watero Yehova.

2 Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Mukupitiriza kuzimwaza ndipo simukuzisamalira.”+

“Tsopano ndikutembenukira kwa inu chifukwa cha zochita zanu zoipazo,”+ watero Yehova.

3 “Ine ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera m’mayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+ 4 Ndidzapatsa nkhosazo abusa ndipo adzaziweta.+ Sizidzaopanso kanthu kapena kugwidwa ndi mantha aakulu,+ ndipo palibe imene idzasowa,” watero Yehova.

5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ 6 M’masiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa,+ ndipo Isiraeli adzakhala mwabata.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.”+

7 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene sadzalumbiranso kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.’+ 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+

9 Mtima wanga wasweka mkati mwanga chifukwa cha aneneri. Mafupa anga onse ayamba kunjenjemera. Ndakhala ngati munthu woledzera,+ komanso mwamuna wamphamvu amene wagonjetsedwa ndi vinyo, chifukwa cha Yehova komanso chifukwa cha mawu ake oyera. 10 Dzikoli ladzaza+ ndi anthu achigololo+ ndipo chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+ ndipo malo a m’chipululu odyetsera ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo.

11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova. 12 “Choncho, njira zawo zidzawakhalira ngati malo oterera+ amdima ndipo adzawakankhira m’njirazo moti adzagwa.”+

“Pakuti ndidzawagwetsera tsoka, tsiku la chilango chawo lidzafika,”+ watero Yehova. 13 “Ndaona zosayenera mwa aneneri a ku Samariya.+ Iwo atumikira ngati aneneri a Baala+ ndipo asocheretsa anthu anga, Aisiraeli.+ 14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.+ Iwo achita chigololo+ ndi kuchita zinthu mwachinyengo.+ Alimbikitsa anthu ochita zoipa kuti aliyense asafooke ndi kusiya+ kuchita zoipa zake. Kwa ine, onsewo akhala ngati Sodomu+ ndipo anthu okhala mumzindawu akhala ngati Gomora.”+

15 Choncho Yehova wa makamu wadzudzula aneneriwo kuti: “Ndiwadyetsa chitsamba chowawa ndipo ndiwamwetsa madzi apoizoni.+ Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko+ wafalikira m’dziko lonse.”

16 Yehova wa makamu wanena kuti: “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa anthu inu.+ Akukulimbikitsani kuchita zinthu zopanda pake.+ Iwo akulankhula masomphenya a mumtima mwawo+ osati ochokera m’kamwa mwa Yehova.+ 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+ 18 Ndani waimirira pagulu la anthu amene Yehova amawakonda+ kuti azindikire ndi kumva mawu ake?+ Ndani watchera khutu kuti amvetsere mawu ake?+ 19 Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova idzawomba. Mkwiyo wake udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu.+ Udzawomba pamitu ya anthu oipawo.+ 20 Mkwiyo wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake+ ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi ndipo mudzazimvetsa.+

21 “Ine sindinatumize aneneriwo, koma okha anathamanga. Ine sindinalankhule nawo, koma okha analosera.+ 22 Ngati iwo akanaima pagulu la anthu amene ndimawakonda,+ akanachititsa anthu anga kumva mawu anga, ndipo akanabweza anthu anga panjira zawo zoipa komanso pa zochita zawo zoipa.”+

23 Yehova wanena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu amene amangokhala pafupi, osati Mulungu amenenso ali kutali?”+

24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova.

“Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. 25 “Ndamva zimene aneneri akulosera monama m’dzina langa+ kuti, ‘Ndalota maloto! Ndalota maloto!’+ 26 Kodi aneneri amene akulosera monamawa, amene akunenera chinyengo cha mumtima mwawo, adzakhala ndi chinyengo chimenechi mumtima mwawo kufikira liti?+ 27 Iwo akuganiza zochititsa anthu anga kuiwala dzina langa pogwiritsa ntchito maloto amene aneneriwo amauzana nthawi zonse,+ monga mmene makolo awo anaiwalira dzina langa chifukwa cha Baala.+ 28 Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, alankhule mawu angawo moona.”+

“Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?”+ watero Yehova.

29 Yehova wanena kuti: “Kodi mawu anga safanana ndi moto?+ Kodi safanana ndi nyundo imene imaphwanya thanthwe?”+

30 “Chotero ndikutsutsana ndi aneneriwo+ chifukwa aliyense wa iwo akuba mawu anga kwa mnzake,”+ watero Yehova.

31 Yehova wanena kuti: “Ine ndikutsutsana ndi aneneriwo chifukwa akugwiritsa ntchito lilime lawo ndi kunena kuti, ‘Awa ndi mawu ochokera kwa Mulungu!’”+

32 “Ine ndikutsutsana ndi aneneri amene akulota maloto onama, amene akunena malotowo ndi kusocheretsa anthu anga ndi bodza lawo+ komanso ndi kudzitama kwawo,”+ watero Yehova.

“Koma ine sindinawatume kapena kuwalamula kuchita zimenezo. Choncho sadzachita zopindulitsa anthu awa,”+ watero Yehova.

33 “Anthu awa, aneneri, kapena ansembe akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga* wa Yehova ukuti chiyani?’+ uwayankhe kuti, ‘“Anthu inu ndinu katundu wolemetsa!+ Ndipo ndidzakusiyani,”+ watero Yehova.’ 34 Mneneri, wansembe, kapena aliyense amene akunena kuti, ‘Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!’ ndidzatembenukira kwa iye ndi kwa nyumba yake.+ 35 Aliyense wa inu akuuza mnzake ndi m’bale wake kuti, ‘Kodi Yehova wayankha kuti chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?’+ 36 Koma anthu inu musanenenso kuti uthenga wa Yehova ndi katundu wolemetsa,+ pakuti mawu a aliyense wa inu ndi katundu wake wolemetsa,+ pakuti mwasintha mawu a Mulungu wathu wamoyo,+ Yehova wa makamu.

37 “Mneneri umufunse kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?+ 38 Ndipo mukapitiriza kunena kuti, “Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!” Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti mukunenabe kuti, ‘Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa,’ pamene ine ndinakuuzani kuti ‘Musamanene kuti: “Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa!”’ 39 tsopano ine ndikukusiyani nokhanokha anthu inu.+ Ndikusiya inuyo ndi mzinda umene ndinapatsa inu ndi makolo anu. Ndikuchita zimenezi kuti musakhalenso pamaso panga.+ 40 Ndidzaika chitonzo pa inu mpaka kalekale ndipo mudzanyozeka mpaka kalekale. Zimenezi sizidzaiwalika.”’”+

24 Ndiyeno Yehova anandisonyeza madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandisonyeza zimenezi Nebukadirezara mfumu ya Babulo atatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri+ ndi omanga makoma achitetezo kuchokera ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+ 2 Nkhuyu zimene zinali m’dengu limodzi zinali zabwino kwambiri ngati nkhuyu zoyamba kucha.+ Koma nkhuyu zimene zinali m’dengu lina zinali zoipa kwambiri moti munthu sakanatha kuzidya chifukwa cha kuipa kwake.

3 Pamenepo Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Yeremiya?” Ndipo ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nkhuyu. Nkhuyu zabwino n’zabwino kwambiri, ndipo nkhuyu zoipa n’zoipa kwambiri moti munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake.”+

4 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: 5 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu otengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo kudziko la Akasidi ndidzawaona ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawatumiza kudziko la Akasidi+ kuchoka m’dziko lino m’njira yabwino.+ 6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino,+ ndipo ndidzawabwezeretsa kudziko lino.+ Pamenepo ndidzawalimbitsa, osati kuwapasula. Ndidzawabzala, osati kuwazula.+ 7 Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo pakuti adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+

8 “‘Chotero mofanana ndi nkhuyu zoipa zija zimene munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake,+ Yehova wanena kuti: “Momwemonso ndidzapereka Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake ndi anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira m’dzikoli,+ komanso anthu okhala m’dziko la Iguputo.+ 9 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho, chifukwa cha masoka aakulu amene ndidzawagwetsera.+ Anthu a mitundu ina adzawatonza, kuwayesa chosereula, kuwanyoza+ ndipo adzakhala otembereredwa+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsirako.+ 10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+

25 Awa ndi mawu amene Yeremiya anauzidwa onena za anthu onse a mu Yuda m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, chimenenso chinali chaka choyamba cha ulamuliro wa Nebukadirezara mfumu ya Babulo. 2 Mneneri Yeremiya analankhula mawu amenewa ponena za anthu onse a mu Yuda komanso ponena za anthu onse okhala mu Yerusalemu kuti:

3 “Kuyambira m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya+ mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero, zaka 23 zonsezi, Yehova wakhala akundiuza mawu ndipo ine ndakhala ndikukuuzani mawuwo, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kukuuzani mawu akewo koma simunandimvere.+ 4 Yehova anakutumizirani atumiki ake onse aneneri. Anali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, koma inu simunawamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti mumvetsere.+ 5 Aneneriwo anali kukuuzani kuti, ‘Chonde, aliyense wa inu atembenuke ndi kusiya njira yake yoipa ndi zochita zake zoipa+ kuti mupitirize kukhala m’dziko limene Yehova anakupatsani, inuyo ndi makolo anu. Anakupatsani dzikoli kuti chikhale cholowa chanu kwa nthawi yaitali.+ 6 Ndipo musatsatire milungu ina kuti muziitumikira ndi kuigwadira. Mukachita zimenezo mudzandikhumudwitsa chifukwa cha mafano anu amene mudzapanga, ndipo ineyo ndidzakugwetserani tsoka.’+

7 “‘Koma simunandimvere,’ watero Yehova, ‘ndipo munachita zimenezo n’cholinga chondikhumudwitsa ndi mafano anu. Zimenezi zakubweretserani tsoka.’+

8 “Choncho Yehova wa makamu wanena kuti, ‘“Popeza simunamvere mawu anga, 9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ watero Yehova, “ndipo ndikuitananso Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mtumiki wanga.+ Ndikuitana anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu okhala mmenemo, komanso kuti aukire mitundu yonse yokuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani, ndi kukusandutsani chinthu chodabwitsa chimene azidzachiimbira mluzu+ ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.+ 10 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala m’malowo.+ Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi.+ Simudzamvekanso kupera kwa mphero+ ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale.+ 11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja, chinthu chodabwitsa, ndipo mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+

12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova. 13 Mawu anga onse amene ndinanena motsutsana ndi dzikolo ndidzawakwaniritsa. Ndidzakwaniritsa zonse zolembedwa m’buku ili, zimene Yeremiya wanenera kuti zidzachitikira mitundu yonse.+ 14 Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu otchuka+ agwiritsa ntchito anthu anga monga antchito awo.+ Chotero ndidzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo ndiponso mogwirizana ndi ntchito za manja awo.’”+

15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Landira chikho ichi chimene chili m’dzanja langa. Mmenemu muli vinyo wa mkwiyo ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako.+ 16 Iwo akamwe ndi kudzandira uku ndi uku ndipo akakhale ngati anthu amisala chifukwa cha lupanga limene ndikuwatumizira pakati pawo.”+

17 Choncho ndinatenga chikho chija chimene chinali m’dzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako.+ 18 Mitunduyo ndi iyi: Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake. Ndinawamwetsa kuti mizinda yawo ikhale bwinja, chinthu chodabwitsa+ chimene anthu azidzachiimbira mluzu, ndiponso kuti ikhale yotembereredwa. Zimenezi zatsala pang’ono kuchitika.+ 19 Ndinamwetsanso Farao mfumu ya Iguputo, atumiki ake, akalonga ake ndi anthu ake onse,+ 20 khamu lonse la anthu a mitundu yosiyanasiyana, mafumu onse a dziko la Uzi,+ mafumu onse a dziko la Afilisiti,+ Asikeloni,+ Gaza,+ Ekironi+ ndi otsala onse a ku Asidodi,+ 21 Edomu,+ Mowabu+ ndi ana a Amoni,+ 22 mafumu onse a Turo,+ mafumu onse a Sidoni+ ndi mafumu a pachilumba cha m’nyanja. 23 Ndinamwetsanso Dedani,+ Tema,+ Buza, onse odulira ndevu zawo zam’mbali,+ 24 mafumu onse a Aluya,+ mafumu onse a anthu a mitundu yosiyanasiyana amene amakhala m’chipululu, 25 mafumu onse a Zimiri, mafumu onse a Elamu,+ mafumu onse a Amedi,+ 26 mafumu onse akumpoto, akutali ndi apafupi, mmodzi ndi mmodzi wa iwo, ndipo ndinamwetsanso maufumu ena onse a padziko lapansi. Mfumu ya Sesaki+ nayonso idzamwa pambuyo pa onsewa.

27 “Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Imwani, muledzere, musanze ndi kugwa osadzukanso+ chifukwa cha lupanga limene ndikukutumizirani pakati panu.”’+ 28 Ngati angakakane kulandira chikhochi m’manja mwako kuti amwe ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mumwabe basi.+ 29 Ndipo taonani! pobweretsa tsoka, ndiyamba ndi mzinda wotchedwa ndi dzina langa.+ Kodi inuyo mukufuna kuti musalandire chilango?”’+

“‘Chilangochi sichikuphonyani pakuti ndikuitana lupanga kuti liukire anthu onse okhala padziko lapansi,’ watero Yehova wa makamu.

30 “Ndiyeno iweyo, unenere mawu onsewa, ndipo anthuwo uwauze kuti, ‘Yehova adzabangula ngati mkango ali kumwamba,+ ndipo adzafuula ali kumalo ake oyera kumene amakhala.+ Iye adzabanguliradi malo ake okhalapo a padziko lapansi. Adzaimbira anthu onse okhala padziko lapansi nyimbo yofanana ndi imene anthu oponda mphesa amaimba.’+

31 “‘Phokoso lidzamveka kumalekezero a dziko lapansi, pakuti Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu.+ Iye mwini adzalimbana ndi anthu onse powaweruza.+ Anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’+ watero Yehova.

32 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Taonani! Tsoka likuyenda kuchokera mu mtundu wina kupita mu mtundu wina,+ ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 33 Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.+ Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda.+ Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’+

34 “Fuulani, ndipo lirani abusa inu!+ Gubuduzikani pafumbi+ inu anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa,+ chifukwa masiku a kuphedwa ndi kubalalitsidwa kwanu afika+ ndipo mudzagwa ndi kuphwanyika ngati chiwiya chosiririka!+ 35 Abusa alibe malo othawirako, ndipo njira yothawira ya anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa yatha.+ 36 Tamverani! Kulira kwa abusa ndi anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa, chifukwa Yehova akuwononga malo awo odyetserako nkhosa. 37 Malo okhalako amtendere asanduka opanda chamoyo chilichonse chifukwa cha mkwiyo woyaka moto wa Yehova.+ 38 Iye watuluka m’malo ake okhalamo ngati mkango wamphamvu wolusa.+ Dziko lawo lasanduka chinthu chodabwitsa chifukwa cha lupanga loopsa komanso chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.”+

26 Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panafika mawu ochokera kwa Yehova akuti: 2 “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire m’bwalo la nyumba ya Yehova,+ ndipo anthu onse amene akubwera kudzalambira panyumba ya Yehova ukawauze zimene zidzachitikira mizinda yonse ya Yuda. Ukawauze mawu onse amene ndidzakulamula kuti uwauze.+ Usachotsepo mawu ngakhale amodzi.+ 3 Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa.+ Pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.+ 4 Choncho uwauze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ngati simudzandimvera mwa kutsatira chilamulo+ chimene ndakupatsani,+ 5 komanso kumvera mawu a atumiki anga aneneri amene ndikuwatumiza kwa inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, amene inu simunawamvere,+ 6 pamenepo ine ndidzachititsa nyumba iyi kukhala ngati nyumba ya ku Silo.+ Ndipo mzinda uwu ndidzausandutsa chinthu chotembereredwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.’”’”+

7 Choncho ansembe, aneneri ndi anthu onse anayamba kumvetsera pamene Yeremiya anali kulankhula mawu amenewa m’nyumba ya Yehova.+ 8 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira ndi kunena kuti: “Ukufa basi.+ 9 N’chifukwa chiyani wanenera m’dzina la Yehova kuti, ‘Nyumba iyi idzafanana ndi nyumba ya ku Silo+ ndipo mzinda uwu udzawonongedwa moti simudzapezeka aliyense wokhalamo’?” Pamenepo anthu onse anali kubwera ndi kuzungulira Yeremiya m’nyumba ya Yehova.

10 Kenako akalonga a Yuda anamva mawu amenewa ndipo anakwezeka kuchokera kunyumba ya mfumu kupita kunyumba ya Yehova.+ Kumeneko anakhala pansi pachipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.+ 11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anayamba kuuza akalongawo ndi anthu onse kuti: “Munthu uyu akuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa chakuti wanenera za mzinda uwu monga mmene mwamvera ndi makutu anu.”+

12 Atatero, Yeremiya anauza akalonga onse ndi anthu onse kuti: “Yehova ndi amene anandituma kuti ndidzanenere mawu onse amene mwamva okhudza nyumba iyi ndi mzinda uwu.+ 13 Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino+ ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake pa tsoka limene wanena kuti akugwetserani.+ 14 Kunena za ine, ndilitu m’manja mwanu.+ Ndichiteni zimene mukuona kuti n’zabwino ndi zoyenera.+ 15 Koma mudziwe kuti, mukandipha mupalamula mlandu wamagazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Mlanduwo ukhala pa inuyo, pamzindawu ndi pa anthu onse okhala mumzindawu+ chifukwa kunena zoona, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onsewa.”+

16 Zitatero, akalonga+ ndi anthu onse anauza ansembe ndi aneneriwo kuti: “Munthu uyu sakuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa walankhula nafe m’dzina la Yehova Mulungu wathu.”+

17 Ndiyeno akuluakulu ena a anthu a m’dzikomo anaimirira ndi kuyamba kuuza mpingo wonse wa anthuwo kuti:+ 18 “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda.+ Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+ 19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova?+ Kodi atatero, Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawagwetsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu.+

20 “Panalinso munthu wina amene anali kunenera m’dzina la Yehova. Iyeyu anali Uliya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-yearimu.+ Iye anali kunenera zimene zidzachitikira mzinda uwu ndi dziko ili mogwirizana ndi mawu onse a Yeremiya. 21 Ndiyeno Mfumu Yehoyakimu,+ asilikali ake onse amphamvu ndi akalonga onse anamva mawu amene Uliya anali kunena. Pamenepo mfumu inakonza zoti imuphe.+ Uliya atamva zimenezo, nthawi yomweyo anachita mantha+ ndipo anathawira ku Iguputo. 22 Koma Mfumu Yehoyakimu inatumiza Elinatani, mwana wa Akibori+ ndi amuna ena ku Iguputo. 23 Kumeneko anthuwo anagwira Uliya ndi kubwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inapha Uliya ndi lupanga+ ndi kutaya mtembo wake m’manda a anthu wamba.”

24 Koma Ahikamu,+ mwana wa Safani+ anali kuteteza Yeremiya kuti anthu asamuphe.+

27 Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya,+ mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti akanene mawu akuti: 2 “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira ndiponso magoli,+ ndipo uzivale m’khosi mwako.+ 3 Kenako, uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya ana a Amoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene akubwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda. 4 Ukatero, uwalamule kuti akauze ambuye awo kuti:

“‘“Mukauze ambuye anu kuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli,+ wanena kuti, 5 ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu+ ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+ 6 Tsopano ndapereka mayiko onsewa m’manja mwa mtumiki wanga+ Nebukadinezara, mfumu ya Babulo.+ Ndamupatsanso nyama zakutchire kuti zimutumikire.+ 7 Choncho mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo,+ mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pamenepo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamugwiritsa ntchito ngati wantchito wawo.’+

8 “‘“‘Ndiyeno mtundu uliwonse wa anthu ndi ufumu umene sudzatumikira Nebukadinezara mfumu ya Babulo, umenenso sudzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo, ine ndidzaulanga ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ kufikira nditaufafaniza kudzera mwa Nebukadinezara,’+ watero Yehova.

9 “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+ 10 Pakuti anthu amenewa akulosera monama kwa inu. Ndipo mukawamvera mudzatengedwa kuchoka m’dziko lanu kupita kudziko lakutali. Ine ndidzakubalalitsani ndipo inu mudzatheratu.+

11 “‘“‘Mtundu wa anthu umene udzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira, ndidzauchititsa kukhala mwamtendere m’dziko lawo, ndipo adzalima minda ndi kukhalabe m’dzikomo,’ watero Yehova.”’”+

12 Zedekiya+ mfumu ya Yuda ndinamuuza mawu onsewa+ kuti: “Ikani makosi anu m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira. Mutumikire mfumuyo ndi anthu ake, kuti mukhalebe ndi moyo.+ 13 Kodi iweyo ndi anthu ako muferenji ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri?+ Izi ndi zimene Yehova wanena kuti zidzachitikira mtundu umene sukutumikira mfumu ya Babulo. 14 Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+

15 “‘Ine sindinawatume,’ watero Yehova, ‘koma iwo akulosera m’dzina langa monama, ndipo mukawamvera ndidzakubalalitsani.+ Inu pamodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inuwo mudzatha.’”+

16 Ndiyeno ndinalankhula ndi ansembe ndi anthu ena onsewa kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya za m’nyumba ya Yehova zibwezedwa kuchokera ku Babulo posachedwapa!”+ Pakuti iwo akulosera kwa inu monama.+ 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mukhale ndi moyo.+ Kodi mzinda uwu ukhale bwinja chifukwa chiyani?+ 18 Koma ngati iwo ndi aneneri, ndipo Yehova wawauza mawu, iwo achonderere kwa Yehova wa makamu+ kuti ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babulo.’

19 “Yehova wa makamu wanena mawu okhudza zipilala,+ thanki ya madzi,*+ zotengera zamawilo+ ndi ziwiya zotsala mumzinda uwu,+ 20 zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasiya pamene anatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+ 21 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu+ kuti, 22 ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo+ ndipo zidzakhala kumeneko kufikira ine nditazikumbukira,”+ watero Yehova. “Ndipo ndidzazibweretsa ndi kuzibwezeretsa pamalo ano.”’”+

28 Ndiyeno m’chaka chimenecho, chaka chachinayi, m’mwezi wachisanu, kuchiyambi kwa ufumu wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, Hananiya+ mwana wa Azuri, mneneri wa ku Gibeoni,+ anauza Yeremiya m’nyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti: 2 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+ 3 Pa zaka ziwiri zokha ndibwezeretsa pamalo ano ziwiya zonse za m’nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo+ anatenga pamalo ano ndi kupita nazo ku Babulo.’” 4 “‘Ndipo Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, ndiponso anthu onse a mu Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo+ ndiwabwezeretsa kuno, pakuti ndithyola goli+ la mfumu ya Babulo,’ watero Yehova.”

5 Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anali chilili m’nyumba ya Yehova,+ 6 inde, Yeremiya anayankha kuti: “Zikhale momwemo!*+ Yehova achitedi zimenezo! Yehova akwaniritse zonse zimene walosera m’mawu ako. Achite zimenezo mwa kubwezeretsa pamalo ano ziwiya za m’nyumba ya Yehova ndi anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo!+ 7 Komabe, tamvera mawu amene ndikufuna kukuuza pamaso pa anthu onse.+ 8 Aneneri akalekale amene analiko ineyo ndisanakhalepo komanso iweyo usanakhalepo+ anali kuloseranso za nkhondo, masoka ndi miliri yoti igwere mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu.+ 9 Koma mneneri amene walosera za mtendere+ amadziwika kuti ndi munthu amene Yehova wamutumadi ulosi wakewo ukakwaniritsidwa.”+

10 Hananiya atamva zimenezo anatenga goli limene linali m’khosi mwa mneneri Yeremiya ndipo analithyola.+ 11 Kenako Hananiya+ anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Pa zaka ziwiri zokha, ndithyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu monga mmene ndathyolera goli ili.’”+ Zitatero, Yeremiya anachokapo.+

12 Mneneri Hananiya atathyola goli limene linali m’khosi mwa mneneri Yeremiya,+ Yehova anauza Yeremiya kuti: 13 “Pita ukauze Hananiya kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wathyola magoli+ amtengo, ndipo tsopano m’malomwake padzakhala magoli achitsulo.”+ 14 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndidzaika magoli achitsulo pamakosi a mitundu ya anthu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya Babulo,+ ndipo ndikunenetsa kuti adzamutumikiradi.+ Nebukadinezara ndidzamupatsanso ngakhale nyama zakutchire.”’”+

15 Pamenepo mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zonama.+ 16 Chotero Yehova wanena kuti, ‘Ndikukuchotsera moyo wako. Chaka chomwe chino iweyo ufa,+ chifukwa zimene wanenazo ndi kupandukira Yehova kwenikweni.’”+

17 Choncho mneneri Hananiya anamwalira chaka chomwecho, m’mwezi wa 7.+

29 Awa ndi mawu a m’kalata imene mneneri Yeremiya anatumiza kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu otsala pakati pa anthu amene anali ku ukapolo, kwa ansembe ndi kwa aneneri. Kalatayi inapitanso kwa anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+ 2 Pamene analemba kalata imeneyi, mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna za panyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu,+ amisiri ndi omanga makoma achitetezo+ anali atatengedwa kupita ku ukapolo kuchokera ku Yerusalemu. 3 Yeremiya anatumiza kalata imeneyi kudzera mwa Elasa mwana wa Safani+ ndi Gemariya mwana wa Hilikiya amene Zedekiya+ mfumu ya Yuda anawatuma ku Babulo kwa Nebukadinezara mfumu ya Babulo. Kalatayo inali ndi mawu akuti:

4 “Kwa anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo, amene Mulungu anawapititsa ku ukapolo ku Babulo+ kuchokera ku Yerusalemu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, akuti, 5 ‘Mangani nyumba ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake.+ 6 Tengani akazi ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi.+ Ana anu aamuna muwapezere akazi ndipo ana anu aakazi muwakwatitse kwa amuna kuti nawonso abereke ana aamuna ndi ana aakazi. Muchulukane, musakhale ochepa ayi. 7 Komanso mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere. Muziupempherera kwa Yehova, pakuti mzindawo ukakhala pa mtendere inunso mudzakhala pa mtendere.+ 8 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu asakunyengeni+ ndipo musamvere anthu amene akufotokoza maloto awo amene alota.+ 9 Pakuti ‘zimene akukuuzanizo akulosera m’dzina langa monama. Ine sindinawatume,’+ watero Yehova.”’”

10 “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwanira muli ku Babulo ndidzakucheukirani anthu inu,+ ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa lokubwezeretsani kumalo ano.’+

11 “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira+ zokupatsani mtendere osati masoka,+ kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’+ watero Yehova. 12 ‘Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’+

13 “‘Inu mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza+ chifukwa mudzandifunafuna ndi mtima wanu wonse.+ 14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ watero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera m’mitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndakubalalitsirani,’+ watero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani ndi kukupititsani ku ukapolo.’+

15 “Koma inu mwanena kuti, ‘Yehova watiutsira aneneri ku Babulo.’

16 “Kwa mfumu imene ikukhala pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso anthu onse okhala mumzinda uwu, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo,+ Yehova akuti, 17 ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndikutumizira anthu amene anatsala ku Yuda lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ ndipo ndidzawachititsa kukhala ngati nkhuyu zophulika zimene munthu sangazidye chifukwa cha kuipa kwake.”’+

18 “‘Ndidzawathamangitsa ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri, ndipo ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+ Ndidzawachititsa kukhala chinthu chotembereredwa, chodabwitsa, chochilizira mluzu ndiponso chotonzedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu a kumene ndidzawabalalitsirako.+ 19 Ndidzawachitira zimenezi chifukwa chakuti sanamvere mawu anga amene ndinali kuwatumizira kudzera mwa atumiki anga aneneri. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kutumiza atumiki angawo,’+ watero Yehova.

“‘Inunso simunandimvere,’+ watero Yehova.

20 “Choncho nonsenu amene muli ku ukapolo,+ amene ndinakuchotsani ku Yerusalemu ndi kukutumizani ku Babulo, imvani mawu awa a Yehova.+ 21 Ponena za Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maaseya amene akulosera m’dzina langa monama pakati panu,+ Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amenewa ndikuwapereka m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, ndipo adzawapha inu mukuona.+ 22 Anthu onse a ku Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, potemberera ena azidzatchula za Zedekiya ndi Ahabu kuti: “Yehova akuchititse kukhala ngati Zedekiya ndi Ahabu+ amene mfumu ya Babulo inawawotcha pamoto!”+ 23 Zimenezi zidzawachitikira chifukwa chakuti akhala akuchita zinthu zopanda nzeru mu Isiraeli,+ ndipo akupitiriza kuchita chigololo ndi akazi a anzawo.+ Komanso akupitiriza kulankhula zonama m’dzina langa. Iwo akulankhula mawu amene sindinawalamule kuti akanene.+

“‘“Ine ndikuzidziwa zimenezi ndipo ndine mboni yake,”+ watero Yehova.’”

24 “Ndiyeno Semaya+ wa ku Nehelamu umuuze kuti, 25 ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Iwe watumiza makalata m’dzina lako+ kwa anthu onse amene ali ku Yerusalemu, kwa Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, ndi kwa ansembe onse. Makalatawo ndi onena kuti, 26 ‘Yehova wakuika kukhala wansembe m’malo mwa Yehoyada wansembe kuti ukhale woyang’anira wamkulu m’nyumba ya Yehova+ ndi kuti umange munthu aliyense wamisala+ amene akuchita zinthu ngati mneneri. Munthu woteroyo umuike m’matangadza, miyendo, manja ndi mutu womwe.+ 27 Nanga n’chifukwa chiyani sunadzudzule Yeremiya wa ku Anatoti,+ amene akuchita zinthu ngati mneneri pakati panu?+ 28 N’chifukwa chake iye watitumizira kalata ku Babulo kuno yonena kuti: “Mukhala akapolo kumeneko kwa nthawi yaitali. Mangani nyumba ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake,+ . . .”’”’”

29 Pamenepo Zefaniya+ wansembe anawerengera mneneri Yeremiya kalata imeneyi.

30 Ndiyeno Yehova anauza Yeremiya kuti: 31 “Anthu onse amene ali ku ukapolo uwatumizire uthenga+ wakuti, ‘Ponena za Semaya wa ku Nehelamu, Yehova wanena kuti: “Pakuti Semaya walosera kwa anthu inu, ngakhale kuti ine sindinamutume, ndipo wayesa kukuchititsani kukhulupirira zinthu zonama,+ 32 Yehova wanena kuti, ‘Ine ndilanga Semaya+ wa ku Nehelamu ndi ana ake.’+

“‘“‘Sipadzapezeka mwamuna wochokera m’banja lake pakati pa anthu awa.+ Ndipo sadzaona zabwino zimene ndichitire anthu anga,+ chifukwa zimene walankhulazo ndi kupandukira Yehova kwenikweni,’+ watero Yehova.”’”

30 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.+ 3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+

4 Awa ndi mawu amene Yehova wauza Isiraeli ndi Yuda. 5 Yehova wanena kuti: “Ife tamva phokoso la anthu amene akunjenjemera. Iwo agwidwa ndi mantha+ ndipo palibe mtendere. 6 Anthu inu, funsani kuti mudziwe ngati mwamuna angabale mwana.+ N’chifukwa chiyani mwamuna aliyense wamphamvu akuoneka atagwira manja m’chiuno ngati mkazi amene akubala mwana? N’chifukwa chiyani nkhope zawo zonse zafooka?+ 7 Kalanga ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu+ moti palibe lofanana nalo.+ Limeneli ndi tsiku la masautso kwa Yakobo.+ Koma adzapulumuka m’masautso amenewa.”

8 “Pa tsikuli ndidzathyola goli ndi kulichotsa m’khosi lanu. Ndidzadula zingwe zimene akumangani nazo,+ moti alendowo sadzagwiritsanso ntchito Yakobo monga wantchito wawo,” watero Yehova wa makamu. 9 “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu+ imene ndidzakuutsirani.”+

10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+

11 “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+

12 Yehova wanena kuti: “Sudzachira kuvulala kwako.+ Chilonda chako cha mkwapulo ndi chosachiritsika.+ 13 Palibe amene akuchonderera kuti chilonda chako chipole.+ Palibe njira iliyonse yokuchiritsira ndipo palibe mankhwala amene angakuthandize.+ 14 Achigololo onse amene anali kukukonda kwambiri akuiwala.+ Iwo sakukufunafunanso. Ndakumenya ndi mkwapulo+ ngati mdani ndipo ndakulanga ngati munthu wankhanza+ chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako.+ Machimo ako achuluka kwambiri.+ 15 N’chifukwa chiyani ukulira pamene wadzivulaza mwadala?+ Ululu wako ndi wosachiritsika chifukwa zolakwa zako zachuluka ndipo machimo ako ndi ochuluka kwambiri.+ Ine ndakuchitira zimenezi. 16 Choncho, onse okuwononga adzawonongedwa,+ ndipo adani ako onse adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Amene akulanda katundu wako nawonso adzalandidwa katundu wawo. Onse ofunkha zinthu zako nawonso zinthu zawo zidzafunkhidwa.”+

17 “Ndidzakubwezeretsa mwakale ndipo ndidzachiritsa zilonda zako za mkwapulo,”+ watero Yehova. “Iwo anakutcha kuti mkazi wothamangitsidwa ndipo anali kunena kuti:+ ‘Ameneyu ndi Ziyoni ndipo palibe amene akumufunafuna.’”+

18 Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu a m’mahema a Yakobo+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pachiunda chake+ ndipo nsanja yokhalamo idzakhala pamalo ake oyenera.+ 19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+ Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+ Ndidzachulukitsa chiwerengero chawo moti sadzakhala kagulu kakang’ono ka anthu.+ 20 Ana ake aamuna adzabwerera mwakale ndipo khamu la anthu ake lidzakhazikika pamaso panga.+ Ndidzalanga onse omupondereza.+ 21 Munthu wotchuka adzachokera mwa iye+ ndipo pakati pa anthu ake padzatuluka wolamulira.+ Ndidzamulola kundiyandikira ndipo adzabwera kwa ine.”+

“Tsopano uyu ndani amene wapereka mtima wake ngati chikole kuti ayandikire kwa ine?”+ watero Yehova. 22 “Inu mudzakhaladi anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.”+

23 Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova yawomba. Mkwiyo wake wawomba ngati kamvulumvulu wosakaza.+ Wawomba pamitu ya anthu oipa.+ 24 Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi.+

31 “Pa nthawi imeneyo ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Isiraeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga,”+ watero Yehova.

2 Yehova wanena kuti: “Anthu amene anapulumuka ku lupanga, ndinawakomera mtima m’chipululu,+ pamene Isiraeli anali kupita kumalo ake ampumulo.”+ 3 Yehova anabwera kwa ine kuchokera kutali, ndipo anati: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale.+ N’chifukwa chake ndakukoka mwa kukoma mtima kwanga kosatha.+ 4 Chotero ndidzakumanganso ndipo udzakhazikika,+ iwe namwali wa Isiraeli. Udzanyamula maseche ndi kupita kukavina pamodzi ndi anthu amene akuseka.+ 5 Udzabzala mpesa kumapiri a ku Samariya.+ Obzala mpesawo adzadya zipatso zake.+ 6 Pakuti tsiku lidzafika, pamene alonda amene ali m’mapiri a Efuraimu adzafuula kuti, ‘Nyamukani amuna inu, tiyeni tipite ku Ziyoni, kwa Yehova Mulungu wathu.’”+

7 Yehova wanena kuti: “Fuulirani Yakobo mosangalala, fuulani kwambiri muli patsogolo pa mitundu ina ya anthu.+ Lengezani zimenezi.+ Tamandani Mulungu ndi kunena kuti, ‘Inu Yehova, pulumutsani anthu anu, otsalira a Isiraeli.’+ 8 Ine ndikuwabweretsa kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Pakati pawo padzakhala anthu akhungu, olumala, akazi apakati komanso akazi amene atsala pang’ono kubereka.+ Adzabwerera kumalo ano ali mpingo waukulu.+ 9 Adzabwera akulira,+ ndipo ndidzayankha kuchonderera kwawo kuti ndiwakomere mtima. Ndidzawayendetsa kupita kuzigwa za madzi.+ Ndidzawayendetsa m’njira zabwino mmene sadzapunthwa. Pakuti ine ndakhala Tate wa Isiraeli,+ ndipo Efuraimu ndi mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa.”+

10 Inu mitundu ya anthu, imvani mawu a Yehova, ndipo mulengeze mawuwo pazilumba zakutali,+ kuti: “Amene wamwaza Isiraeli ndiye adzamusonkhanitsanso+ ndipo adzamusunga mmene m’busa amasungira nkhosa zake.+ 11 Pakuti Yehova adzawombola Yakobo,+ ndipo adzamutenganso kumuchotsa m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo.+ 12 Pamenepo iwo adzabwera ndi kufuula mosangalala pamwamba pa phiri la Ziyoni.+ Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa Yehova.+ Zidzawalanso chifukwa cha mbewu, vinyo watsopano,+ mafuta, ana a nkhosa ndi ana a ng’ombe.+ Moyo wawo udzakhala ngati munda wothiriridwa bwino+ ndipo sadzakhalanso ofooka.”+

13 “Pa nthawi imeneyo, namwali, anyamata ndi amuna achikulire, onse pamodzi adzasangalala ndipo adzavina.+ Ndidzawachotsera chisoni chawo, moti kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo ndipo ndidzawatonthoza ndi kuwasangalatsa.+ 14 Ansembe ndidzawatsitsimutsa ndi chakudya chochuluka,+ ndipo anthu anga ndidzawakhutiritsa ndi ubwino wanga,”+ watero Yehova.

15 “Yehova wanena kuti, ‘Mawu amveka ku Rama.+ Kwamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni.+ Rakele+ akulirira ana ake.+ Iye wakana kutonthozedwa pamene akulirira ana ake,+ chifukwa ana akewo kulibenso.’”+

16 Yehova wanena kuti: “‘Tonthola, usalire. Usagwetsenso misozi,+ pakuti ulandira mphoto ya ntchito zako,’ watero Yehova, ‘ndipo anawo adzabwerera kuchokera kudziko la mdani.’+

17 “‘Uli ndi tsogolo labwino+ ndipo ana ako adzabwerera kudziko lawo,’+ watero Yehova.”

18 “Ndamva Efuraimu akudzilirira+ kuti, ‘Mwandidzudzula kuti ndiwongolere.+ Ndinali ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa.+ Ndithandizeni kubwerera ndipo ndidzabwereradi,+ pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.+ 19 Nditabwerera kwa inu ndinadzimvera chisoni.+ Mutandithandiza kuzindikira ndinadzimenya pantchafu chifukwa cha chisoni.+ Ndinachita manyazi ndipo ndinanyazitsidwa+ chifukwa cha chitonzo cha paubwana wanga.’”+

20 “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa?+ Pamlingo umene ndalankhula zomulanga, ndidzakumbukira kumuchitira zabwino pamlingo womwewo.+ N’chifukwa chake m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye.+ Mosalephera ndidzamumvera chisoni,”+ watero Yehova.

21 “Udziikire zizindikiro za mumsewu. Udziikire zikwangwani.+ Ika mtima wako panjirayo, njira imene uyenera kuyendamo.+ Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.+ 22 Kodi udzapatukira uku ndi uku kufikira liti,+ iwe mwana wamkazi wosakhulupirika?+ Yehova walenga chinthu chatsopano padziko lapansi. Chinthucho n’chakuti, mkazi wamba adzakupatira mwamuna wamphamvu.”

23 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanena mawu awa m’dziko la Yuda ndi m’mizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe+ malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+ 24 Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhala pamodzi m’dzikolo. Mudzakhalanso alimi ndi anthu oweta ziweto.+ 25 Pakuti ndidzatsitsimutsa wolefuka ndipo ndidzalimbitsa wofooka aliyense.”+

26 Pamenepo, ndinagalamuka ndi kuyamba kuona. Ndinali nditagona tulo tokoma.

27 “Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachititsa nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda kukhalanso ndi anthu ochuluka ndiponso ziweto zochuluka,” watero Yehova.+

28 “Monga mmene ndakhalira ndikufunafuna mpata+ kuti ndiwazule, kuwagwetsa, kuwapasula, kuwawononga ndi kuwasakaza,+ ndidzakhalanso nawo tcheru kuti ndiwamange ndi kuwabzala,”+ watero Yehova. 29 “Masiku amenewo sadzanenanso kuti, ‘Abambo ndiwo anadya mphesa yosapsa koma mano a ana awo ndiwo anayayamira.’*+ 30 Koma munthu aliyense adzafa chifukwa cha zolakwa zake.+ Mano a munthu aliyense wodya mphesa yosapsa ndiwo adzayayamira.”

31 “Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachita pangano latsopano+ ndi nyumba ya Isiraeli+ komanso ndi nyumba ya Yuda,”+ watero Yehova. 32 “Koma pangano limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo.+ ‘Pangano langa limenelo analiphwanya+ ngakhale kuti ine ndinali mwamuna wawo,’+ watero Yehova.”

33 “Pangano+ limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili:+ Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo+ ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,”+ watero Yehova.

34 “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake+ kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’+ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu,”+ watero Yehova. “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”+

35 Yehova ndiye Wopereka dzuwa kuti liziwala masana,+ woikira mwezi malamulo,+ wopereka nyenyezi+ kuti ziziwala usiku,+ amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Wochita zimenezi dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye wanena kuti: 36 “‘Ngati malamulo amenewa angachotsedwe pamaso panga,+ ndiye kuti anthu amene ndi mbewu ya Isiraeli sadzakhala mtundu wokhala pamaso panga nthawi zonse,’+ watero Yehova.”

37 Yehova wanena kuti: “‘Ngati kumwamba kungayezedwe ndipo ngati maziko a dziko lapansi angafufuzidwe,+ inenso ndingakane anthu onse amene ndi mbewu ya Isiraeli chifukwa cha zonse zimene achita,’+ watero Yehova.”

38 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene anthu adzamangira+ Yehova mzinda kuyambira pa Nsanja ya Hananeli+ mpaka ku Chipata cha Pakona.+ 39 Chingwe choyezera+ chidzachokera kumeneko n’kulunjika kuphiri la Garebi ndipo chidzazungulira mpaka ku Gowa. 40 Chigwa chonse cha mitembo+ ndi cha phulusa+ losakanizika ndi mafuta, masitepe onse mpaka kukafika kuchigwa cha Kidironi,+ mpaka kukona ya Chipata cha Hatchi+ moyang’anana ndi kotulukira dzuwa, zidzakhala zoyera kwa Yehova.+ Mzindawu sudzazulidwa ndipo sudzapasulidwanso mpaka kalekale.”+

32 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya m’chaka cha 10 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda.+ Chimenechi chinali chaka cha 18 cha Nebukadirezara.+ 2 Pa nthawi imeneyo, magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu.+ Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera m’nyumba imene inali m’Bwalo la Alonda.+ Bwalo limeneli linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda. 3 Anam’tsekera kumeneko chifukwa Zedekiya mfumu ya Yuda sanafune kuti Yeremiya azinenera,+ moti anamuuza kuti:

“N’chifukwa chiyani ukulosera+ kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa mfumu ya Babulo moti iulanda,+ 4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m’manja mwa Akasidi, pakuti adzaperekedwa ndithu m’manja mwa mfumu ya Babulo moti adzalankhulana ndi kuonana maso ndi maso ndi mfumuyo?”’+ 5 Ukuloseranso kuti, ‘Mfumu ya Babulo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko kufikira nditamucheukira,’+ watero Yehova. Ukunenanso kuti, ‘ngakhale kuti anthu inu mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’ N’chifukwa chiyani ukulosera zimenezi?”+

6 Ndiyeno Yeremiya anati: “Yehova wandiuza kuti, 7 ‘Kukubwera Hanameli mwana wa Salumu m’bale wa bambo ako, kudzakuuza kuti: “Ugule munda wanga wa ku Anatoti+ chifukwa iweyo ndi amene uli ndi ufulu wogula mundawo.”’”+

8 Ndiyeno Hanameli mwana wa m’bale wa bambo anga analowa m’Bwalo la Alonda+ ndipo anandipeza mogwirizana ndi mawu a Yehova. Pamenepo iye anati: “Gula munda wanga wa ku Anatoti,+ m’dziko la Benjamini,+ pakuti iweyo ndi amene uli ndi ufulu woulandira monga cholowa ndiponso uli ndi ufulu wougula. Uugule ndithu.” Atatero ndinadziwa kuti mawu amenewa anali a Yehova.+

9 Zitatero ndinagula munda wa Hanameli+ mwana wa m’bale wa bambo anga. Mundawu unali ku Anatoti.+ Ndinamuyezera ndalama zake+ ndipo zinakwana masekeli* 7 ndi ndalama 10 zasiliva. 10 Ndinalemba chikalata cha pangano+ ndi kuikapo chidindo,+ ndipo ndinaitana mboni+ kuti zidzasaine chikalatacho. Kenako ndinamuyezera+ ndalamazo pasikelo. 11 Ndiyeno mogwirizana ndi malamulo ndi malangizo, ndinatenga chikalata cha pangano chomata ndi chosamata.+ 12 Kenako ndinapereka chikalata cha pangano chogulira mundawo kwa Baruki+ mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya. Ndinamupatsa chikalata chimenechi pamaso pa Hanameli mwana wa m’bale wa bambo anga, pamaso pa mboni zimene zinasaina chikalatacho+ ndi pamaso pa Ayuda onse amene anali m’Bwalo la Alonda.+

13 Ndiyeno ndinalamula Baruki anthu onse akumva, kuti: 14 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Tenga zikalata zimenezi, chikalata cha pangano chomata chogulira munda, ndi chikalata chosamatacho.+ Zimenezi uziike m’mbiya kuti zikhale kwa nthawi yaitali.’ 15 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘M’dziko lino anthu adzagula nyumba, minda ndi minda ya mpesa.’”+

16 Nditapereka chikalata chimenechi kwa Baruki+ mwana wa Neriya,+ ndinapemphera+ kwa Yehova kuti: 17 “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu yanu+ ndi dzanja lanu lotambasula.+ Nkhaniyi si yovuta kwa inu.+ 18 Inu mumasonyeza anthu masauzande ambiri kukoma mtima kosatha.+ Mumabwezera zolakwa za abambo kwa ana awo.*+ Inu ndinu Mulungu woona, wamkulu+ ndi wamphamvu,+ ndipo dzina lanu+ ndinu Yehova wa makamu.+ 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+ 20 Inu munachita zizindikiro ndi zozizwitsa m’dziko la Iguputo. Zimene munachitazo zikudziwikabe mpaka pano mu Isiraeli ndiponso pakati pa anthu onse.+ Munachita zimenezo kuti mudzipangire dzina mofanana ndi zimene mukufuna kuchita posachedwapa.+ 21 Inu munatulutsa anthu anu Aisiraeli m’dziko la Iguputo+ pogwiritsa ntchito zizindikiro, zozizwitsa,+ dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi zinthu zochititsa mantha kwambiri.+

22 “Patapita nthawi munawapatsa dziko lino, limene munalumbirira makolo awo kuti mudzawapatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 23 Iwo analowa m’dzikoli ndi kulitenga kukhala lawo,+ koma sanamvere mawu anu ndi kuyenda motsatira malamulo anu.+ Zinthu zonse zimene munawalamula kuti achite sanachite,+ chotero mwawagwetsera masoka onsewa.+ 24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+ 25 Koma inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, mwandiuza kuti, ‘Gula mundawu ndi ndalama+ pamaso pa mboni,’+ ngakhale kuti mzindawu uperekedwa m’manja mwa Akasidi.”+

26 Pamenepo Yehova anauza Yeremiya kuti: 27 “Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse.+ Kodi kwa ine pali nkhani ina iliyonse yovuta?+ 28 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa Akasidi ndi m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, ndipo aulanda.+ 29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu abwera kudzayatsa moto mzindawu kuti upseretu.+ Ayatsanso nyumba zawo chifukwa pamadenga ake amafukizirapo nsembe zautsi kwa Baala ndipo amathira nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+

30 “‘Ana a Isiraeli ndi ana a Yuda akhala akuchita zoipa pamaso panga kuyambira pa ubwana wawo.+ Ana a Isiraeli akundikhumudwitsa ndi ntchito za manja awo,’+ watero Yehova. 31 ‘Mzinda uwu wakhala chinthu chondikwiyitsa+ ndi chondipsetsa mtima kuyambira pamene unamangidwa kufikira lero. Choncho ndiuchotsa pamaso panga,+ 32 chifukwa cha zoipa zonse zimene ana a Isiraeli+ ndi ana a Yuda+ achita ndi kundikhumudwitsa nazo.+ Achita zimenezi pamodzi ndi mafumu awo,+ akalonga awo,+ ansembe awo,+ aneneri awo,+ amuna a mu Yuda ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu. 33 Iwo anali kundifulatira, sanandiyang’ane.+ Ngakhale kuti ndinali kuwaphunzitsa, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwaphunzitsa, palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anamvetsera kuti alandire mwambo.*+ 34 Iwo anaika zinthu zawo zonyansa m’nyumba imene imatchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+ 35 Kuwonjezera apo anamangira Baala+ malo okwezeka m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Anachita izi kuti azidutsitsa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto monga nsembe+ kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule zimenezi+ ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga kuchita chinthu chonyansa chimenechi,+ kuti Yuda achite tchimo.’+

36 “Tsopano ponena za mzinda uwu umene anthu inu mukunena kuti uperekedwa ndithu m’manja mwa mfumu ya Babulo kuti uwonongedwe ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri,+ Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, 37 ‘Inetu ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa m’dziko lino ndi kuwachititsa kukhala mwamtendere.+ 38 Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+ 39 Ndidzawapatsa mtima umodzi+ ndi kuwachititsa kuyenda m’njira imodzi kuti azindiopa nthawi zonse. Ndidzatero kuti iwo pamodzi ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino.+ 40 Ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale+ lakuti sindidzasiya kuwachitira zabwino+ ndipo ndidzawapatsa mtima woti azindiopa kuti asachoke kwa ine.+ 41 Ndidzakondwera nawo ndi kuwachitira zabwino.+ Ndidzawabzala m’dziko lino+ mokhulupirika ndi mtima wanga wonse komanso ndi moyo wanga wonse.’”

42 “Yehova wanena kuti, ‘Monga mmene ndabweretsera anthu awa masoka aakulu onsewa, momwemonso ndidzawabweretsera zabwino zonsezi zimene ndikunena kuti ndidzawabweretsera.+ 43 Anthu adzagula minda m’dziko lino,+ dziko limene anthu inu mudzanena kuti: “Dziko ili ndi bwinja,+ lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yoweta. Linaperekedwa m’manja mwa Akasidi.”’+

44 “‘Anthu adzagula minda ndi ndalama ndipo padzakhala kulemberana zikalata za pangano+ pamaso pa mboni ndi kumata zikalatazo.+ Zimenezi zidzachitika m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu,+ m’mizinda ya Yuda,+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa+ ndi m’mizinda ya kum’mwera.+ Zidzakhala choncho chifukwa chakuti ndidzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’+ watero Yehova.”

33 Yeremiya atamutsekera m’Bwalo la Alonda,+ Yehova analankhula naye kachiwiri kuti: 2 “Yehova Wopanga+ dziko lapansi, Yehova Woumba+ dzikoli ndi kulikhazikitsa.+ Mulungu amene dzina lake ndi Yehova,+ wanena kuti, 3 ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani.+ Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+

4 “Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba za mumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda zimene zagwetsedwa podziteteza ku ziunda zomenyerapo nkhondo ndiponso ku lupanga la adani.+ 5 Wanenanso mawu okhudza amuna amene akubwera kudzamenyana ndi Akasidi, ndiponso okhudza malo amene adzaza ndi mitembo ya amuna amene wawapha chifukwa cha mkwiyo wake waukulu,+ amenenso ali oipa kwambiri moti iye wausiya mzindawu chifukwa cha kuipa kwa anthu amenewo.+ 6 Iye wanena kuti: ‘Ine ndichiritsa anthu a mumzindawu ndi kuwapatsa thanzi labwino.+ Ndiwachiritsa ndi kuwapatsa mtendere wochuluka ndi choonadi.+ 7 Ndibwezeretsa anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo ndiwalimbitsa kuti akhale ngati mmene analili poyamba.+ 8 Ndiwayeretsa ku zolakwa zawo zonse zimene anachimwa nazo pamaso panga,+ ndipo ndiwakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nazo ndi kuphwanya nazo malamulo anga.+ 9 Mzindawu udzakhala ndi dzina limene lidzandikondweretsa,+ dzina lochititsa kuti nditamandidwe ndi kulandira ulemerero pakati pa mitundu yonse ya padziko lapansi imene idzamva za zinthu zabwino zimene ndikuwachitira.+ Anthu a mitundu inawo adzachita mantha+ ndi kunjenjemera+ chifukwa cha zinthu zabwino ndi mtendere wonse umene ndikubweretsa pamzindawu.’”+

10 “Yehova wanena kuti, ‘Anthu inu mudzanena za dziko lino kuti ndi lopanda pake chifukwa mulibe anthu ndi ziweto. Mudzanena zimenezi za mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu imene yawonongeka,+ moti mulibe anthu ndipo simukukhala munthu aliyense ngakhale ziweto.+ 11 M’malo amenewa mudzamveka mawu achikondwerero ndi achisangalalo.+ Mudzamveka mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi, ndi mawu a anthu onena kuti: “Tamandani Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale!”’+

“‘Anthuwo azidzabweretsa nsembe yoyamikira kunyumba ya Yehova,+ pakuti ndidzabwezeretsa anthu a m’dzikoli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’+ watero Yehova.”

12 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’dziko lino lopanda pake, lopanda anthu ndi lopanda ziweto+ ndi mizinda yake yonse, mudzakhala malo odyetserako ziweto kumene abusa adzalola ziweto zawo kugona pansi.’+

13 “Yehova wanena kuti, ‘Ziweto zidzadutsa pansi pa dzanja la munthu woziwerenga+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa,+ m’mizinda ya kum’mwera,+ m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu+ ndi m’mizinda ya Yuda.’”+

14 “‘Taonani! Masiku adzafika+ pamene ndidzakwaniritsa lonjezo langa+ lokhudza nyumba ya Isiraeli+ ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova. 15 M’masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira yolungama+ ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo m’dzikoli.+ 16 M’masiku amenewo, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu adzatchedwa kuti, Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.’”+

17 “Yehova wanena kuti, ‘M’nyumba ya Davide simudzasowa munthu wokhala pampando wachifumu wa nyumba ya Isiraeli.+ 18 Ndipo ponena za ansembe achilevi, pakati pawo sindidzasowa mwamuna wopereka nsembe zopsereza zathunthu, nsembe yambewu yofukiza komanso nsembe zina nthawi zonse.’”+

19 Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 20 “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale usana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti usana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+ 21 ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi atumiki anga, ansembe achilevi.+ 22 Ine ndidzachulukitsa mbewu ya Davide mtumiki wanga ndi Alevi amene akunditumikira.+ Ndidzawachulukitsa mofanana ndi makamu akumwamba amene sangathe kuwerengedwa ndiponso mofanana ndi mchenga umene munthu sangathe kuuyeza.’”+

23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yeremiya kuti: 24 “Kodi sunamve zimene ena mwa anthu awa akunena kuti, ‘Mabanja awiri amene Yehova wasankha,+ adzawakananso’? Adani akuchitira anthu anga zachipongwe+ ndipo sakuwaonanso ngati mtundu wa anthu.

25 “Yehova wanena kuti, ‘Monga momwedi ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale usana ndi usiku,+ malamulo anga akumwamba ndi dziko lapansi,+ 26 momwemonso sindidzakana mbewu ya Yakobo ndi mbewu ya Davide mtumiki wanga,+ kuti pakati pa mbewu yake nditengepo olamulira mbewu ya Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Pakuti ndidzasonkhanitsa onse amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+

34 Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene Nebukadirezara mfumu ya Babulo,+ gulu lake lonse lankhondo,+ maufumu onse a padziko lapansi, maulamuliro amene anali m’manja mwake+ ndiponso pamene mitundu yonse ya anthu inali kumenyana ndi mzinda wa Yerusalemu, ndi mizinda yonse yozungulira mzindawo.+ Iye anati:

2 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Pita ukauze Zedekiya mfumu ya Yuda,+ kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ine ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo idzautentha.+ 3 Iweyo sudzazemba kuti asakugwire chifukwa adzakugwira ndithu ndi kukupereka m’manja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo+ maso ndi maso, ndipo idzalankhula nawe ndi kupita nawe ku Babulo.’ 4 Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda,+ imva mawu a Yehova akuti, ‘Ponena za iwe, Yehova wanena kuti: “Sudzafa ndi lupanga. 5 Udzafa mu mtendere.+ Anthu adzakufukizira zinthu zonunkhira+ ngati mmene anachitira ndi makolo ako, mafumu amene analipo iwe usanabadwe.+ Polira maliro ako adzanena kuti,+ ‘Kalanga ine mbuyanga!’+ pakuti ‘Ine ndalankhula mawu amenewa,’ watero Yehova.”’”’”

6 Pamenepo mneneri Yeremiya anauza Zedekiya, mfumu ya Yuda, mawu onsewa+ ali ku Yerusalemu. 7 Anamuuza mawu amenewa pamene magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali kumenyana ndi Yerusalemu ndi mizinda ina yonse ya mu Yuda,+ kuphatikizapo Lakisi+ ndi Azeka.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndipo ndi imene inali isanawonongedwe pamizinda ya mu Yuda.+

8 Yehova anauza Yeremiya mawu pamene Mfumu Zedekiya inachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze ufulu,+ 9 kuti aliyense wa iwo amasule wantchito wake wamwamuna kapena wamkazi, mwamuna wachiheberi+ kapena mkazi wachiheberi ndi kumulola kupita kwawo mwaufulu. Anachita izi kuti anthuwo asagwiritsenso ntchito Myuda mnzawo, amene ndi m’bale wawo ngati wantchito wawo.+ 10 Choncho akalonga onse+ anamvera, chimodzimodzinso anthu onse amene anachita pangano kuti aliyense wa iwo alole wantchito wake wamwamuna kapena wamkazi kupita kwawo mwaufulu. Anamvera ndi kuwalola kuchoka kuti asawagwiritsenso ntchito monga atumiki awo.+ 11 Koma pambuyo pake, iwo anatembenuka+ ndi kuyamba kutenganso amuna ndi akazi antchitowo amene anawalola kupita kwawo mwaufulu ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito monga antchito awo aamuna ndi aakazi.+ 12 Pamenepo Yehova anauza Yeremiya mawu, ndipo Yehova anati:

13 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndinachita pangano ndi makolo anu+ pamene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ kumene munali akapolo.+ Ndinapangana nawo kuti: 14 “Kumapeto kwa zaka 7, aliyense wa inu, azimasula m’bale wake,+ Mheberi+ amene anagulitsidwa kwa inu+ ndiponso amene wakutumikirani kwa zaka 6. Muzimulola kuchoka mwaufulu kuti apite kwawo.” Koma makolo anu sanandimvere ndipo sanatchere khutu lawo.+ 15 Koma inu munatembenuka ndi kuchita zolungama pamaso panga mwa kulengeza ufulu, aliyense kwa mnzake. Munachita pangano pamaso panga,+ m’nyumba imene ikutchedwa ndi dzina langa.+ 16 Kenako mwatembenukanso+ ndi kuipitsa dzina langa+ komanso aliyense wa inu watenganso wantchito wake wamkazi ndi wamwamuna amene munawalola kuchoka mwaufulu, zimenenso iwo anagwirizana nazo. Inu mwawatenganso kukhala antchito anu aamuna ndi antchito anu aakazi.’+

17 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Inu simunamvere mawu anga moti simunapitirize kulengeza ufulu,+ aliyense kwa m’bale wake ndi kwa mnzake. Tsopano ine ndikulengeza ufulu kwa inu,’+ watero Yehova. ‘Inu mudzafa ndi lupanga,+ mliri+ ndi njala yaikulu.+ Ndidzakusandutsani chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+ 18 Anthu amene akupatuka pa pangano langa+ mwa kusatsatira mawu a m’pangano limene iwo anachita pamaso panga, ndidzawapereka kwa adani. Iwo anachita pangano limeneli mwakudula pakati+ mwana wa ng’ombe wamphongo ndi kudutsa pakati pake.+ 19 Amene apatuka pa panganoli ndi akalonga a Yuda, akalonga a Yerusalemu,+ nduna za panyumba ya mfumu, ansembe ndi anthu onse a m’dzikoli amene anadutsa pakati pa mwana wa ng’ombe wodulidwa pakatiyo . . . 20 Anthu amenewa ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa onse ofuna moyo wawo.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.+ 21 Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda+ ndi akalonga ake ndidzawapereka m’manja mwa adani awo, m’manja mwa anthu ofuna moyo wawo ndiponso m’manja mwa magulu ankhondo a mfumu ya ku Babulo+ amene akubwerera osakuthirani nkhondo.’+

22 “Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikulamula ndi kubweretsanso adaniwo kumzinda uno.+ Iwo adzamenyana ndi mzindawu ndipo adzaulanda ndi kuutentha.+ Pamenepo, mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa bwinja ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.’”+

35 M’masiku a Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti: 2 “Pita kunyumba ya Arekabu,+ ndipo ukalankhule nawo ndi kubwera nawo kunyumba ya Yehova. Ukalowe nawo m’chimodzi mwa zipinda zodyera ndipo ukawapatse vinyo kuti amwe.”

3 Pamenepo ndinatenga Yaazaniya, mwana wa Yeremiya mwana wa Habaziniya, pamodzi ndi abale ake. Ndinatenganso ana ake onse aamuna ndi mabanja onse a Arekabu. 4 Onsewa ndinawabweretsa m’nyumba ya Yehova. Ndinalowa nawo m’chipinda chodyera+ cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu woona. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda chodyera cha akalonga chimene chinali pamwamba pa chipinda chodyera cha Maaseya mwana wa Salumu,+ amene anali mlonda wa pakhomo. 5 Kenako ndinaika makapu odzaza vinyo ndi zipanda pamaso pa ana a Rekabu ndi kuwauza kuti: “Imwani vinyoyu.”

6 Koma iwo anati: “Sitingamwe vinyo, chifukwa Yonadabu mwana wa Rekabu,+ kholo lathu, anatilamula kuti, ‘Inuyo kapena ana anu musamamwe vinyo mpaka kalekale.+ 7 Musamamange nyumba, musamafese mbewu, musamabzale mpesa kuti ukhale wanu. Muzikhala m’mahema masiku onse a moyo wanu kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi limene mukukhala monga alendo.’+ 8 Choncho ife timamvera mawu a Yehonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu, pa chilichonse chimene anatilamula.+ Timachita zimenezi mwa kupewa kumwa vinyo masiku onse a moyo wathu, ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi.+ 9 Sitimanga nyumba zoti tikhalemo ndipo sitibzala mpesa, kulima minda kapena kubzala mbewu kuti zikhale zathu. 10 Timakhala m’mahema ndipo timamvera ndi kutsatira zonse zimene Yonadabu,+ kholo lathu linatilamula.+ 11 Koma pamene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anabwera kudzaukira dzikoli+ tinati, ‘Tiyeni tilowe mu Yerusalemu chifukwa kukubwera magulu ankhondo a Akasidi ndi magulu ankhondo a ku Siriya. Tiyeni tikakhale mu Yerusalemu.’”+

12 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yeremiya kuti: 13 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Pita ukalankhule ndi anthu a ku Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti: “Kodi inu simunali kulimbikitsidwa nthawi zonse kuti muzimvera mawu anga?”+ watero Yehova. 14 “Anthu a m’nyumba ya Rekabu akhala akutsatira mawu a Yehonadabu mwana wa Rekabu,+ amene analamula ana ake kuti asamwe vinyo, ndipo sanamwe vinyo kufikira lerolino. Iwo achita zimenezi chifukwa chomvera lamulo la kholo lawo.+ Koma ine ndinali kulankhula nanu anthu inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kulankhula nanu,+ koma simunandimvere.+ 15 Ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri,+ kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza. Ndinali kuwatuma uthenga wakuti, ‘Bwererani chonde, aliyense asiye njira zake zoipa+ ndipo sinthani zochita zanu kuti zikhale zabwino.+ Musatsatire milungu ina ndi kuitumikira.+ Mupitirize kukhala m’dziko limene ndinakupatsani, inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera.+ 16 Ana a Yehonadabu mwana wa Rekabu+ atsatira lamulo limene kholo lawo linawalamula,+ koma anthu awa sanandimvere.”’”+

17 “Choncho Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Tsopano Yuda ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiwagwetsera masoka onse amene ndanena.+ Ndichita zimenezi chifukwa ndalankhula nawo koma sanandimvere ndipo ndinali kuwaitana koma sanandiyankhe.’”+

18 Ndiyeno Yeremiya anauza anthu a m’nyumba ya Rekabu kuti: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti mwamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu,+ ndipo mukupitiriza kusunga malamulo ake onse ndi kuchita zonse zimene anakulamulani,+ 19 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sipadzasowa munthu wa m’banja la Yonadabu mwana wa Rekabu woima+ pamaso panga kuti azinditumikira nthawi zonse.”’”+

36 Ndiyeno m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti: 2 “Tenga mpukutu+ ndi kulembamo mawu onse+ amene ndakuuza okhudza chilango chimene ndidzapatsa Isiraeli, Yuda+ ndi mitundu yonse ya anthu.+ Ulembe mawu onse amene ndakuuza kuchokera nthawi imene ndinalankhula nawe m’masiku a Yosiya kufikira lero.+ 3 Mwina anthu a m’nyumba ya Yuda adzamva za masoka onse amene ndikufuna kuwagwetsera+ ndipo aliyense abwerera ndi kusiya njira yake yoipa.+ Akatero, ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndi machimo awo.”+

4 Ndiyeno Yeremiya anaitana Baruki+ mwana wa Neriya kuti adzamuuze mawu onse amene Yehova anauza Yeremiyayo ndi kuti Baruki alembe mawuwo mumpukutu.+ 5 Pamenepo Yeremiya anauza Baruki kuti: “Ine anditsekera ndipo sindingathe kukalowa m’nyumba ya Yehova.+ 6 Choncho iweyo upite kukawerenga mokweza mawu a mumpukutu. Ukawerenge mawu amene walembamo, mawu a Yehova+ amene ndakuuza. Ukawerenge mokweza pamaso pa anthu onse m’nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya.+ Ukawerengenso pamaso pa anthu onse a ku Yuda amene akubwera kuchokera m’mizinda yawo.+ 7 Mwina ukatero Yehova adzamva pempho lawo lakuti awakomere mtima+ ndipo aliyense adzabwerera kusiya njira yake yoipa,+ chifukwa Yehova wanena kuti adzasonyeza anthu awa mkwiyo wake waukulu ndi ukali wake.”+

8 Choncho Baruki+ mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamulamula, kuti apite kunyumba ya Yehova kukawerenga mokweza mawu a Yehova olembedwa mumpukutumo.+

9 Ndiyeno m’chaka chachisanu cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 9,+ analengeza kuti anthu onse a mu Yerusalemu ndi anthu onse amene anali kubwera ku Yerusalemu kuchokera m’mizinda ya Yuda asale kudya pamaso pa Yehova.+ 10 Tsopano Baruki anayamba kuwerenga mpukutuwo mokweza pamaso pa anthu onse. Anayamba kuwerenga mawu onse a Yeremiya panyumba ya Yehova. Anachita izi m’chipinda chodyera+ cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba,+ m’bwalo lakumtunda, pakhomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.+

11 Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani,+ anamva mawu onse a Yehova amene anali mumpukutumo. 12 Pamenepo anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda chodyera cha mlembi, kumene akalonga onse anali atakhala pansi. Kumeneko kunali Elisama+ mlembi, Delaya+ mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya+ mwana wa Safani,+ Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse. 13 Atafika kumeneko Mikaya+ anawauza mawu onse amene anamva pamene Baruki anawerenga mokweza mumpukutu pamaso pa anthu onse.+

14 Zitatero, akalonga onse anatumiza Yehudi+ mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusa, kukaitana Baruki+ kuti: “Tenga mpukutu umene wawerenga mokweza pamaso pa anthu onse ndipo ubwere nawo kuno.” Pamenepo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo ndi kupita kwa iwo.+ 15 Ndiyeno akalongawo anamuuza kuti: “Khala pansi, ndipo uwerenge mokweza kuti timve.” Choncho Baruki+ anawawerengera mpukutuwo mokweza.

16 Tsopano atamva mawu onsewa anayang’anana mwamantha, ndipo anauza Baruki kuti: “Ndithu, tikauza mfumu mawu onsewa.”+ 17 Kenako anafunsa Baruki kuti: “Tiuze, zatheka bwanji kuti ulembe mawu onsewa kuchokera pakamwa pake?”+ 18 Pamenepo Baruki anawauza kuti: “Iye anali kundiuza mawu onsewa ndipo ine ndinali kulemba mumpukutuwu ndi inki.”+ 19 Zitatero, akalongawo anauza Baruki kuti: “Pita, iweyo ndi Yeremiya mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene mwapita.”+

20 Akalongawo anasiya mpukutuwo m’chipinda chodyera+ cha Elisama+ mlembi. Kenako analowa m’bwalo+ kuti akaonane ndi mfumu, ndipo anayamba kuuza mfumu nkhani yonse yokhudza mpukutuwo.

21 Mfumu itamva zimenezi inatuma Yehudi+ kuti akatenge mpukutuwo. Iye anakatenga mpukutuwo m’chipinda chodyera cha Elisama+ mlembi,+ moti Yehudiyo anayamba kuwerenga mokweza pamaso pa mfumu ndi akalonga onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo. 22 Pa nthawiyi mfumu inali itakhala m’nyumba imene inali kukhala m’nyengo yozizira,+ ikuwotha moto wa mumbaula.+ Umenewu unali mwezi wa 9.*+ 23 Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena zinayi za mpukutuwo, mfumu inali kudula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi ndi kuponya chidutswacho pamoto umene unali mumbaula. Inachita izi kufikira mpukutu wonsewo itauponya pamotopo.+ 24 Iwo sanachite mantha+ ndipo mfumu ndi atumiki ake onse amene anali kumvetsera mawu amenewa sanang’ambe zovala zawo.+ 25 Ngakhale kuti Elinatani,+ Delaya+ ndi Gemariya+ anachonderera mfumu kuti isatenthe mpukutuwo, mfumuyo sinawamvere.+ 26 Komanso mfumu inalamula Yerameeli mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti akagwire Baruki mlembi ndi mneneri Yeremiya,+ koma Yehova anawabisa.+

27 Mfumu itatentha mpukutu umene unali ndi mawu amene Baruki+ analemba mouzidwa ndi Yeremiya,+ Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 28 “Tenga mpukutu wina ndipo ulembemo mawu onse amene anali mumpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda yatentha.+ 29 Ponena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe watentha mpukutu+ ndi kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani walemba mumpukutuwu+ kuti: “Mfumu ya Babulo idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndipo simudzapezeka nyama ndi munthu wokhalamo”?’+ 30 Choncho ponena za chilango chimene adzapatsa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sipadzapezeka mwana wake aliyense wokhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mtembo wake adzautaya kunja+ kumene udzakhala padzuwa lotentha masana ndipo usiku udzakhala kunja kozizira. 31 Ine ndidzaimba mlandu Yehoyakimu,+ ana ake ndi atumiki ake chifukwa cha zolakwa zawo.+ Anthu amenewa komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndi anthu a mu Yuda ndidzawagwetsera masoka onse amene ndanena.+ Ngakhale kuti ndawauza za masoka onsewa iwo sanamvere.’”’”+

32 Pamenepo Yeremiya anatenga mpukutu wina ndi kuupereka kwa Baruki mlembi,+ mwana wa Neriya. Baruki analembamo mawu onse amene Yeremiya anamuuza,+ mawu onse amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha.+ Mumpukutumo anawonjezeramo mawu ena ambiri ofanana ndi a mumpukutu woyamba uja.

37 Ndiyeno Mfumu Zedekiya+ mwana wa Yosiya,+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anamuika kukhala mfumu m’dziko la Yuda,+ anayamba kulamulira m’malo mwa Koniya+ mwana wa Yehoyakimu.+ 2 Koma Zedekiyayo, atumiki ake ndi anthu a m’dzikoli sanamvere mawu amene Yehova+ ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya.+

3 Mfumu Zedekiya inatumiza Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya+ wansembe kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga wakuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.”+ 4 Yeremiya anali kukhala mwaufulu pakati pa anthu+ chifukwa anali asanamutsekere m’ndende. 5 Ndiyeno gulu lankhondo la Farao linabwera kuchokera ku Iguputo.+ Akasidi amene anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu atamva zimenezi anachoka ku Yerusalemu.+ 6 Kenako Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti: 7 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu inu mukauze mfumu ya Yuda imene yakutumani kuno kudzafunsira uthenga wa Mulungu kwa ine+ kuti: “Taonani! Gulu lankhondo la Farao limene likubwera kwa anthu inu kuti likuthandizeni lidzabwerera kwawo ku Iguputo.+ 8 Ndipo Akasidi adzabweranso ndithu kudzamenyana ndi mzinda uno, kuulanda ndi kuutentha ndi moto.”+ 9 Yehova wanena kuti: “Musadzinyenge+ pomanena kuti, ‘Akasidi amenewa samenyana nafe, achoka ndithu,’ chifukwa sachoka ayi. 10 Pakuti ngakhale anthu inu mutapha gulu lonse lankhondo la Akasidi amene akumenyana nanu+ ndipo pangotsala amuna ovulala kwambiri pakati pawo,+ aliyense wa amenewo adzadzuka muhema wake ndi kubwera kudzatentha mzinda uno.”’”

11 Ndiyeno gulu lankhondo la Akasidi litabwerera kuchoka ku Yerusalemu+ chifukwa cha gulu lankhondo la Farao,+ 12 Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita kudziko la Benjamini+ kuti akalandire malo ake pakati pa anthu ake. 13 Atafika pa Chipata cha Benjamini,+ anakumana ndi mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya. Nthawi yomweyo Iriya anagwira mneneri Yeremiya ndi kunena kuti: “Ukuthawira kwa Akasidi!” 14 Yeremiya anamuyankha kuti: “Zabodza zimenezo!+ Ine sindikuthawira kwa Akasidi.” Koma Iriya sanamumvere. Choncho iye anagwirabe Yeremiya ndi kumubweretsa kwa akalonga. 15 Pamenepo akalonga+ anamukwiyira kwambiri Yeremiya+ ndipo anamumenya+ ndi kumutsekera m’ndende+ m’nyumba ya Yehonatani+ mlembi, pakuti nyumba yake ndi imene anaisandutsa ndende.+ 16 Yeremiya atalowa m’ndende ya pansiyo,+ m’kachipinda ka m’ndendemo, anakhala mmenemo kwa masiku ambiri.

17 Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya. Atabwera naye, mfumuyo inayamba kumufunsa mafunso m’nyumba mwake pamalo obisika.+ Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Pamenepo Yeremiya anayankha kuti: “Inde alipo!” Ndiyeno Yeremiya ananenanso kuti: “Inuyo mudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Babulo!”+

18 Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti: “Kodi ineyo ndakulakwirani chiyani pamodzi ndi atumiki anu ndiponso anthu onse,+ kuti munditsekere m’ndende? 19 Tsopano ali kuti aneneri anu amene anali kulosera kwa inu ponena kuti, ‘Mfumu ya Babulo sidzabwera kudzamenyana ndi anthu inu ndiponso kudzamenyana ndi dzikoli’?+ 20 Tsopano ndimvereni chonde, mbuyanga mfumu. Chonde, mverani pempho langa lakuti mundikomere mtima.+ Musandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ mlembi, chifukwa ndingakafere kumeneko.”+ 21 Chotero Mfumu Zedekiya inalamula kuti atsekere Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndipo anali kumupatsa mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate+ ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

38 Ndiyeno Sefatiya mwana wa Mateni, Gedaliya mwana wa Pasuri, Yukali+ mwana wa Selemiya ndi Pasuri mwana wa Malikiya+ anamva mawu onse amene Yeremiya anali kuuza anthu onse+ kuti: 2 “Yehova wanena kuti, ‘Amene adzapitirize kukhala mumzinda uno adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ kapena mliri.+ Koma amene adzadzipereke kwa Akasidi adzakhala ndi moyo. Adzapulumutsa moyo wake, sadzafa ayi.’+ 3 Yehova wanena kuti, ‘Mzinda uno udzaperekedwa ndithu m’manja mwa gulu lankhondo la mfumu ya Babulo, ndipo mfumuyo idzaulanda ndithu.’”+

4 Pamenepo akalonga anayamba kuuza mfumu kuti: “Chonde lolani kuti munthu uyu aphedwe,+ chifukwa iye akufooketsa amuna ankhondo amene atsala mumzinda uno, pamodzi ndi anthu onse, mwa kuwauza mawu amenewa.+ Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.” 5 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inawayankha kuti: “Taonani! Iye ali m’manja mwanu. Palibe chimene ine mfumu ndingachite motsutsana nanu.”+

6 Chotero iwo anagwira Yeremiya ndi kumuponya m’chitsime cha Malikiya+ mwana wa mfumu, chimene chinali m’Bwalo la Alonda.+ Iwo anatsitsira Yeremiya m’chitsimemo ndi zingwe. M’chitsimemo munalibe madzi koma munali matope, ndipo Yeremiya anayamba kumira m’matopemo.+

7 Tsopano Ebedi-meleki Mwitiyopiya,*+ amene anali nduna m’nyumba ya mfumu, ndipo pa nthawiyo anali m’nyumbamo, anamva kuti Yeremiya amuponya m’chitsime. Apa n’kuti mfumu itakhala pansi ku Chipata cha Benjamini.+ 8 Choncho Ebedi-meleki anatuluka m’nyumba ya mfumuyo ndipo anapita kwa mfumu kukaiuza kuti: 9 “Inu mbuyanga mfumu, zimene anthu awa achitira mneneri Yeremiya ndi zoipa, chifukwa amuponya m’chitsime, ndipo afera momwemo+ chifukwa cha njala,+ pakuti mkate watheratu mumzindawu.”

10 Pamenepo mfumu inalamula Ebedi-meleki Mwitiyopiya kuti: “Tenga amuna 30 kunoko, ndipo mukamutulutse mneneri Yeremiya m’chitsimemo asanafe.”+ 11 Chotero Ebedi-meleki anatenga amunawo ndipo iye analowa m’nyumba ya mfumu, kumunsi kwa malo osungirako chuma.+ Kumeneko anatenga nsanza ndi zidutswa zotha ntchito zansalu. Zimenezi anazitsitsira m’chitsime kwa Yeremiya+ pogwiritsa ntchito zingwe. 12 Ndiyeno Ebedi-meleki Mwitiyopiya anauza Yeremiya kuti: “Kulunga zingwezo ndi nsanza komanso ndi zidutswa za nsalu ndipo uziike m’khwapa.” Yeremiya anachitadi zomwezo.+ 13 Zitatero anatulutsa Yeremiya m’chitsimemo ndi zingwe. Ndipo Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

14 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inatumiza anthu kuti akatenge mneneri Yeremiya ndi kubwera naye kwa iye+ pakhomo lachitatu+ la m’nyumba ya Yehova.+ Yeremiya atafika, mfumu inamuuza kuti: “Ndikufuna ndikufunse. Usandibisire kalikonse.”+ 15 Pamenepo Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Kodi ndikakuuzani simundipha? Komanso ndikakulangizani, simundimvera ayi.”+ 16 Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya, ali pamalo obisika kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene amatipatsa moyo,+ sindikupha ndipo sindikupereka m’manja mwa anthu awa amene akufuna moyo wako.”+

17 Pamenepo Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova Mulungu wa makamu,+ Mulungu wa Isiraeli,+ wanena kuti, ‘Mukadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzinda uwu sadzautentha, komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+ 18 Koma ngati simudzadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo, ndiye kuti mzinda uno udzaperekedwa m’manja mwa Akasidi ndipo adzautentha.+ Inuyo simudzapulumuka m’manja mwawo.’”+

19 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inauza Yeremiya kuti: “Ndikuopa Ayuda amene athawira kwa Akasidi.+ Ndikuopa kuti Akasidi andipereka m’manja mwawo ndipo Ayudawo andizunza.”+ 20 Koma Yeremiya anati: “Sadzakuperekani m’manja mwawo mwa njira imeneyo. Chonde, mverani mawu a Yehova amene ndikukuuzani. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino+ ndipo mudzakhalabe ndi moyo. 21 Koma ngati mukukana kutuluka+ kuti mukadzipereke, Yehova wandisonyeza izi: 22 Taonani! Akazi onse amene atsala m’nyumba ya mfumu ya Yuda+ akutuluka nawo panja kupita nawo kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ ndipo akaziwo akunena kuti,

‘Amuna amene unali kukhala nawo pa mtendere akunyengerera+ ndipo akugonjetsa.+

Achititsa kuti mapazi ako amire m’matope ndipo iwo abwerera ndipo akusiya.’+

23 “Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akutuluka nawo panja kupita nawo kwa Akasidi, ndipo inuyo simudzapulumuka m’manja mwa Akasidiwo,+ koma dzanja la mfumu ya Babulo lidzakugwirani. Mzinda uno adzautentha chifukwa cha inu.”+

24 Pamenepo Zedekiya anauza Yeremiya kuti: “Munthu aliyense asadziwe zimenezi, kuti usafe. 25 Ngati akalonga+ angamve kuti ndalankhula nawe, ndipo abwera kwa iwe ndi kukuuza kuti, ‘Chonde tiuze, unali kulankhula zotani ndi mfumu? Usatibisire kalikonse, ndipo sitikupha. Nanga mfumu yakuuza chiyani?’ 26 Uwauze kuti, ‘Ndinali kupempha mfumu kuti indikomere mtima, ndipo isandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ chifukwa ndingakafere kumeneko.’”

27 Patapita nthawi, akalonga onse anafika kwa Yeremiya ndipo anayamba kumufunsa mafunso. Yeremiya anawayankha mogwirizana ndi mawu onsewa amene mfumu inamulamula.+ Choncho akalongawo anakhala chete pamaso pake chifukwa sanamve zimene anakambirana. 28 Yeremiya anapitirizabe kukhala m’Bwalo la Alonda+ kufikira tsiku limene Yerusalemu analandidwa.+ Mawu a Yeremiya anakwaniritsidwadi pamene Yerusalemu analandidwa.+

39 M’chaka cha 9 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 10,+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anafika ku Yerusalemu ndi kuzungulira mzindawo.+

2 M’chaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya, m’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9, anaboola mpanda wa mzindawo.+ 3 Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindamo ndi kukhala pansi ku Chipata cha Pakati.+ Mayina a akalongawo anali Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.

4 Ndiyeno Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse ankhondo ataona adaniwo anayamba kuthawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo analowera njira ya kumunda wa mfumu,+ kukatulukira pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, n’kupitiriza kuthawa molowera ku Araba.+ 5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+ 6 Zitatero mfumu ya Babulo inapha+ ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona.+ Inaphanso akuluakulu onse a ku Yuda.+ 7 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga m’maunyolo amkuwa kuti apite naye ku Babulo.

8 Akasidi anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu onse.+ Iwo anagwetsanso mpanda wa Yerusalemu.+ 9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+

10 Ndiyeno ena mwa anthuwo, anthu onyozeka amene analibe kalikonse, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawasiya m’dziko la Yuda,+ ndipo pa tsiku limenelo anawapatsa minda ya mpesa ndi ntchito zokakamiza kuti azigwira.+

11 Kuwonjezera pamenepo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo anapereka lamulo lokhudza Yeremiya kwa Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, kuti: 12 “Mtenge uzimuyang’anira ndipo usamuchitire choipa chilichonse.+ Koma uzimuchitira chilichonse chimene iye wanena.”+

13 Pamenepo Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu pamodzi ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi, Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14 Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndi kumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake, kuti Yeremiyayo akakhale pakati pa anthu akwawo.

15 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene anali wotsekeredwa m’Bwalo la Alonda.+ Iye anamuuza kuti: 16 “Pita kwa Ebedi-meleki+ Mwitiyopiya ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndiugwetsera tsoka osati zinthu zabwino.+ Pa tsikulo zimene ndinanena zidzachitika iwe ukuona.”’+

17 “‘Pa tsikulo ndidzakulanditsa+ ndipo sudzaperekedwa m’manja mwa anthu amene umawaopa,’+ watero Yehova.

18 “‘Pakuti ine ndidzakupulumutsa ndithu, ndipo sudzaphedwa ndi lupanga, koma udzapulumutsa moyo wako+ chifukwa chakuti wandikhulupirira,’+ watero Yehova.”

40 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya, pamene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anamumasula ku Rama.+ Yeremiya anali womangidwa maunyolo a m’manja pamene Nebuzaradani anamutenga pakati pa anthu a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anali kupita ku ukapolo ku Babulo.+ 2 Ndiyeno mkulu wa asilikaliyu anatenga Yeremiya ndi kumuuza kuti: “Yehova Mulungu wako ananeneratu za tsoka ili limene lagwera dziko lino.+ 3 Yehova ananena za tsoka limeneli moti anatsimikiza kukwaniritsa zimene ananenazo. Anatero chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamvere mawu ake. Choncho monga mmene ukuoneramu, zimenezi zachitikadi.+ 4 Tsopano taona! Lero ndakumasula maunyolo amene anali m’manja mwako. Ngati ungakonde kutsagana nane ku Babulo tiye, ndipo ndidzakuyang’anira.+ Koma ngati sungakonde kutsagana nane ku Babulo, tsala. Taona! Dziko lonse lili pamaso pako. Pita kulikonse kumene ungaone kuti n’kwabwino, kulikonse kumene ungakonde kupita.”+

5 Koma Yeremiya anali asanaganize zobwerera pamene Nebuzaradani anamuuza kuti: “Bwerera kwa Gedaliya,+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ amene mfumu ya Babulo yamuika kukhala wolamulira mizinda ya Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu ako ndipo ukapite kulikonse kumene ungakonde kupita.”+

Pamenepo mkulu wa asilikali olondera mfumu anamupatsa chakudya chapaulendo ndi mphatso ndipo anamulola kupita.+ 6 Chotero Yeremiya anapita ku Mizipa+ kukakhala ndi Gedaliya+ mwana wa Ahikamu pakati pa anthu amene anatsala m’dzikolo.

7 Patapita nthawi, akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali m’madera a kunja kwa mzinda+ pamodzi ndi anthu awo, anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala wolamulira dzikolo. Anamvanso kuti yamuika kuti azilamulira amuna, akazi, ana ndi anthu onyozeka m’dzikolo amene sanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babulo.+ 8 Choncho akuluakulu amenewa anapita kwa Gedaliya ku Mizipa. Mayina awo anali Isimaeli+ mwana wa Netaniya, Yohanani+ ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti, ana a Efai Mnetofa,+ Yezaniya+ mwana wa Amaakati+ pamodzi ndi asilikali awo.+ 9 Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani+ analumbira+ pamaso pa akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kutumikira Akasidi. Pitirizani kukhala m’dzikoli n’kumatumikira mfumu ya Babulo ndipo zinthu zikuyenderani bwino.+ 10 Ine ndikhala ku Mizipa+ kuno kuti ndizikuimirani kwa Akasidi amene adzabwera kwa ife. Koma inu, sonkhanitsani vinyo,+ zipatso za m’chilimwe* ndi mafuta ndi kuziika m’ziwiya zanu ndipo muzikhala m’mizinda imene mwaitenga kukhala yanu.”

11 Pamenepo Ayuda onse amene anali kukhala ku Mowabu, amenenso anali kukhala pakati pa ana a Amoni, amene anali ku Edomu ndi ena amene anali m’mayiko ena onse+ anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya+ mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kukhala wolamulira anthu otsala ku Yuda. 12 Ndiyeno Ayuda onse anayamba kubwerera kuchokera kumadera onse kumene anathawira. Anali kubwera m’dziko la Yuda kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Iwo anasonkhanitsa vinyo ndi zipatso za m’chilimwe zochuluka kwambiri.

13 Nayenso Yohanani+ mwana wa Kareya+ ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali m’madera a kunja kwa mzinda,+ anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. 14 Iwo anauza Gedaliya kuti: “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni+ watumiza Isimaeli+ mwana wa Netaniya+ kuti adzakuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanakhulupirire zimenezo.+

15 Ndiyeno Yohanani+ mwana wa Kareya anauza Gedaliya pamalo obisika ku Mizipa kuti: “Ndikufuna kupita tsopano lino kukapha Isimaeli mwana wa Netaniya pakuti palibe amene adzadziwa.+ N’chifukwa chiyani iyeyo akufuna kukupha? N’chifukwa chiyani akufuna kuti anthu onse a mu Yuda amene akubwera kwa iwe amwazike, ndi kuti anthu otsala mu Yuda awonongeke?”+ 16 Koma Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ anauza Yohanani mwana wa Kareya kuti: “Usachite zimenezi. Zimene ukunena zokhudza Isimaeli si zoona.”+

41 Tsopano m’mwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama,+ anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10.+ Isimaeli anali wa m’banja lachifumu+ ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Atafika kumeneko anayamba kudya chakudya pamodzi.+ 2 Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna 10 amene anali naye ananyamuka ndi kukapha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani. Choncho Isimaeli anapha munthu amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.+ 3 Isimaeli anaphanso Ayuda onse amene anali ndi Gedaliya ku Mizipa pamodzi ndi Akasidi, amuna ankhondo, amene anawapeza kumeneko.

4 Pa tsiku lachiwiri kuchokera pamene Gedaliya anaphedwa, munthu aliyense asanadziwe zimenezi,+ 5 kunabwera amuna ochokera ku Sekemu,+ ku Silo+ ndi ku Samariya.+ Iwo analipo 80 ndipo anabwera atameta ndevu,+ atadzichekacheka ndiponso atang’amba zovala zawo.+ Amunawa anabwera ndi nsembe yambewu ndi lubani+ m’manja mwawo kuti adzazipereke kunyumba ya Yehova. 6 Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ananyamuka ku Mizipa akulira kuti akakumane nawo.+ Atakumana nawo anawauza kuti: “Tiyeni kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu.” 7 Koma anthuwo atafika pakati pa mzinda, Isimaeli mwana wa Netaniya anawapha ndi kuwaponya m’chitsime. Iye anapha anthuwa mothandizana ndi amuna amene anali naye.+

8 Tsopano pakati pa anthuwo panali amuna 10 amene anauza Isimaeli mofulumira kuti: “Usatiphe, pakuti tili ndi chuma chobisika m’munda. Tili ndi tirigu, barele, mafuta ndi uchi.”+ Chotero Isimaeli anawasiya ndipo sanawaphe mmene anachitira ndi abale awo. 9 Chitsime chimene Isimaeli+ anaponyamo mitembo yonse ya amuna amene anawapha chinali chachikulu kwambiri. Mfumu Asa ndi imene inakumba chitsime chimenechi pamene Basa mfumu ya Isiraeli inamuopseza.+ Chitsime chimenechi ndi chimene Isimaeli mwana wa Netaniya anaponyamo mitembo ya anthu amene anawapha.

10 Kenako Isimaeli anagwira anthu onse otsala, ana aakazi a mfumu,+ amene anali ku Mizipa.+ Anagwiranso anthu ena onse otsala ku Mizipa+ amene Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawapereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu+ kuti aziwayang’anira. Chotero Isimaeli mwana wa Netaniya anawagwira ndipo ananyamuka kuti awolokere nawo kudziko la ana a Amoni.+

11 Patapita nthawi, Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo+ amene anali naye anamva zoipa zonse zimene Isimaeli mwana wa Netaniya anachita. 12 Choncho iwo anatenga amuna onse ndi kupita kukamenyana ndi Isimaeli mwana wa Netaniya. Iwo anamupeza pafupi ndi madzi ambiri a ku Gibeoni.+

13 Ndiyeno anthu onse amene anali ndi Isimaeli ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye, anayamba kusangalala kwambiri. 14 Anthu onse amene Isimaeli anawagwira ku Mizipa+ anatembenuka ndi kuthawira kwa Yohanani mwana wa Kareya. 15 Koma Isimaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi amuna 8 anathawa+ ataona Yohanani. Iye anathawira kwa ana a Amoni.

16 Ndiyeno Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa. Anthu amenewa anawalanditsa m’manja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Analanditsa amuna amphamvu, amuna ankhondo, akazi awo, ana ndi nduna za panyumba ya mfumu. Yohanani analanditsa anthu amenewa ku Gibeoni. 17 Iwo anakakhala kumalo ogona a Chimamu pafupi ndi Betelehemu+ ndi cholinga choti apitirize ulendo wawo kukalowa mu Iguputo.+ 18 Anachita zimenezi chifukwa cha Akasidi.+ Iwo anali kuopa Akasidiwo+ chifukwa chakuti Isimaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu+ amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.+

42 Kenako akuluakulu onse a magulu ankhondo, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya+ mwana wa Hoshaya+ ndi anthu onse osasiyapo aliyense, anapita 2 kwa mneneri Yeremiya ndi kumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako.+ Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa amene tatsala tilipo ochepa monga mmene ukutioneramu, ngakhale kuti tinalipo anthu ambiri.+ 3 Ndipo Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.”+

4 Pamenepo mneneri Yeremiya anawayankha kuti: “Ndamva zimene mwanenazo. Ndipemphera kwa Yehova Mulungu wanu malinga ndi zimene mwapempha.+ Ndipo mawu aliwonse amene Yehova angakuyankheni ndidzakuuzani.+ Sindidzakubisirani kalikonse.”+

5 Ndiyeno iwo anauza Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange+ ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi mawu onse amene Yehova Mulungu wako angakutume kwa ife.+ 6 Kaya mawu a Yehova Mulungu wathu ndi otikomera kapena otiipira, ife tidzamvera mawuwo. Tidzatero kuti zinthu zitiyendere bwino chifukwa chomvera mawu a Yehova Mulungu wathu.”+

7 Tsopano patapita masiku 10, Yehova analankhula ndi Yeremiya.+ 8 Kenako Yeremiya anaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye. Anaitananso anthu ena onse osasiyapo aliyense.+ 9 Iye anawauza kuti: “Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli kukamupempha kuti akukomereni mtima.+ Tsopano iye wanena kuti, 10 ‘Ngati mungakhalebe m’dziko lino,+ ndidzakulimbitsani osati kukupasulani, ndidzakubzalani osati kukuzulani,+ pakuti ndidzakumverani chisoni chifukwa cha tsoka limene ndakugwetserani.+ 11 Musachite mantha ndi mfumu ya Babulo imene mukuiopayo.’+

“‘Mfumu imeneyi musachite nayo mantha,+ chifukwa ine ndili ndi inu kuti ndikupulumutseni ndi kukulanditsani m’manja mwake,’+ watero Yehova. 12 Ndidzakuchitirani chifundo moti mfumuyo idzakumverani chifundo ndi kukubwezerani kudziko lanu.+

13 “‘Koma ngati munganene kuti: “Ayi! Ife sitikhala m’dziko lino,” kumene ndi kusamvera mawu a Yehova Mulungu wanu,+ 14 ndipo mukapitiriza kunena kuti: “Ife tikupita kukakhala ku Iguputo,+ kumene sitidzaona nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga komanso kumene sitidzasowa chakudya, moti tikupita kukakhala kudziko limenelo,”+ 15 mverani mawu a Yehova, inu otsala a Yuda. Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ngati mwatsimikiza mtima kukakhala ku Iguputo ndipo mwalowadi m’dzikolo ndi kukhala kumeneko monga alendo,+ 16 ndiye kuti lupanga limene mukuliopa lidzakupezani ku Iguputo+ komweko ndipo njala yaikulu imene mukuithawa idzakutsatirani ku Iguputoko+ moti mudzafera komweko.+ 17 Amuna onse amene atsimikiza mtima kukakhala ku Iguputo monga alendo ndiwo adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri.+ Pakati pawo sipadzapezeka wopulumuka kapena wothawa chifukwa ndidzawagwetsera tsoka.”’+

18 “Yehova Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Monga mmene ndinasonyezera anthu okhala mu Yerusalemu+ mkwiyo ndi kupsa mtima kwanga, inunso ndidzakusonyezani mkwiyo wanga chifukwa chakuti mwakakhala ku Iguputo. Mudzakhala otembereredwa ndipo mudzakhala chinthu chodabwitsa ndi chotonzedwa,+ moti malo ano simudzawaonanso.’+

19 “Yehova wakutsutsani inu otsala a Yuda. Musapite ku Iguputo.+ Ine ndikuchitira umboni lero+ 20 kuti mwachimwira miyoyo yanu.+ Zili choncho chifukwa inu mwandituma kwa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu ndipo udzatiuze zilizonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndipo ife tidzachita zomwezo.’+ 21 Koma inu simudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu kapena chilichonse chimene wandituma chimene ndakuuzani lero.+ 22 Tsopano dziwani kuti, ndithu mudzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu ndi mliri m’dziko limene mukulakalaka kukalowamo kuti mukakhale monga alendo kumeneko.”+

43 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kuuza anthu onse mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova Mulungu anatuma Yeremiya kukawauza,+ 2 Azariya mwana wa Hoshaya,+ Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu enanso odzikuza+ anauza Yeremiya kuti: “Ukunena zabodza. Yehova Mulungu wathu sanakutume kudzatiuza+ kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko monga alendo.’+ 3 Koma Baruki+ mwana wa Neriya ndiye akukulimbikitsa kunena zinthu zofuna kutipweteketsa ndi cholinga chotipereka m’manja mwa Akasidi kuti atiphe kapena kutitenga kupita ku ukapolo ku Babulo.”+

4 Chotero Yohanani mwana wa Kareya, akuluakulu onse a magulu ankhondo ndi anthu onse sanamvere mawu a Yehova+ kuti apitirize kukhala m’dziko la Yuda,+ 5 moti Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo anatenga otsala a Yuda amene anabwerera kuchokera ku mitundu yonse ya anthu kumene anathawira kuti akhale m’dziko la Yuda kwa kanthawi kochepa.+ 6 Anatenga amuna amphamvu, akazi awo, ana aang’ono, ana aakazi a mfumu+ ndiponso aliyense amene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu analola kuti akhale ndi Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani.+ Anatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki+ mwana wa Neriya. 7 Pamapeto pake anafika ku Iguputo+ chifukwa sanamvere mawu a Yehova ndipo patapita nthawi anakafika ku Tahapanesi.+

8 Tsopano pamene Yeremiya anali ku Tahapanesi, Yehova anamuuza kuti: 9 “Tenga miyala ikuluikulu ndipo ukaibise m’dothi limene anamangira chiunda cha njerwa chimene chili pakhomo la nyumba ya Farao ku Tahapanesi. Ukachite zimenezi amuna onse achiyuda akuona.+ 10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Inetu ndikuitana Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala iyi imene ndaibisa. Iye adzamanga hema wake waulemerero pamwamba pa miyala imeneyi. 11 Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+ 12 Nyumba za milungu ya Iguputo ndidzaziyatsa moto.+ Nebukadirezara adzatentha milunguyo ndi kuitenga kupita nayo kudziko lina. Monga mmene m’busa savutikira kuvala chovala chake,+ Nebukadirezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo ndi kuchokako atapambana. 13 Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu ya Iguputo adzazitentha.”’”

44 Mulungu anauza Yeremiya uthenga woti akauze Ayuda onse amene anali kukhala m’dziko la Iguputo,+ m’madera a Migidoli,+ Tahapanesi,+ Nofi+ ndi Patirosi.+ Uthengawo unali wakuti: 2 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi yakhala mabwinja ndipo palibe amene akukhalamo.+ 3 Izi zachitika chifukwa cha zinthu zoipa zimene mwachita ndi kundikhumudwitsa nazo. Mwafukiza nsembe zautsi+ ndi kutumikira milungu ina imene inu kapena makolo anu simunaidziwe.+ 4 Ine ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza.+ Ndinali kuwatuma uthenga wakuti: “Chonde, musachite zinthu zonyansa zoterezi zimene ndimadana nazo.”+ 5 Koma inu simunamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti musiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina.+ 6 Choncho ndasonyeza mkwiyo wanga ndi ukali wanga ndipo watentha mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu.+ Lero malo amenewa ndi owonongeka ndipo asanduka bwinja.’+

7 “Tsopano Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukudziitanira tsoka lalikulu?+ Kodi simukudziwa kuti muphetsa amuna, akazi, ana aang’ono ndi ana oyamwa+ pakati pa Yuda, moti sipapezeka wotsala aliyense? 8 Mukudziitanira tsoka mwa kundilakwira ndi ntchito za manja anu. Mukuchita zimenezi mwa kufukiza nsembe zautsi kwa milungu ina+ m’dziko la Iguputo limene munalowamo kuti mukhale monga alendo. Mudziphetsa chifukwa cha zimenezi ndipo mudzakhala otembereredwa ndi otonzedwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.+ 9 Kodi mwaiwala zoipa zimene makolo anu anachita?+ Kodi mwaiwala zoipa za mafumu a Yuda+ ndi za akazi awo,+ zoipa zanu ndi za akazi anu,+ zimene munachita m’dziko la Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu? 10 Simunadzichepetse kufikira lero+ ndipo simunachite mantha,+ kapena kutsatira malamulo+ ndi malangizo amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.’+

11 “Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndakukanani* ndipo ndikugwetserani tsoka ndi kupha anthu onse a mu Yuda.+ 12 Ine ndigwira otsala a Yuda amene anatsimikiza mtima kulowa m’dziko la Iguputo ndi kukhala mmenemo monga alendo,+ moti onse adzathera m’dziko la Iguputo.+ Iwo adzakanthidwa ndi lupanga ndipo onsewo, osasiyapo aliyense, adzatha chifukwa cha njala yaikulu.+ Adzafa ndi lupanga komanso njala yaikulu. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chodabwitsa ndi chotonzedwa.+ 13 Ndidzalanga onse okhala m’dziko la Iguputo monga mmene ndinalangira Yerusalemu. Ndidzawalanga ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri.+ 14 Sipadzapezeka aliyense wothawa kapena wopulumuka mwa otsala a Yuda amene alowa m’dziko la Iguputo ndi kukhala mmenemo monga alendo,+ kupatulapo anthu ochepa chabe amene adzathawa. Sipadzapezeka wobwerera kudziko la Yuda kumene akulakalaka kubwerera kuti akakhaleko.’”+

15 Ndiyeno amuna onse amene anali kudziwa kuti akazi awo anali kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina,+ akazi onse amene anaimirira ndi kupanga mpingo waukulu, komanso anthu onse amene anali kukhala ku Iguputo+ m’dera la Patirosi,+ anayankha Yeremiya kuti: 16 “Ife sitimvera mawu amene watiuza m’dzina la Yehova.+ 17 Ife tichita zonse zimene tanena.+ Tipereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa+ kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Tichita zimenezi monga mmene ife,+ makolo athu,+ mafumu athu+ ndi akalonga athu anachitira m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pamene tinali kudya mkate ndi kukhuta ndipo zinthu zinali kutiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse.+ 18 Ndipotu kuyambira pamene tinasiya kupereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa ‘mfumukazi yakumwamba,’+ chilichonse chikutisowa, ndipo tawonongeka chifukwa cha lupanga ndi njala yaikulu.+

19 “Komanso popereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa ‘mfumukazi yakumwamba,’+ kodi sitinafunse amuna athu popangira mfumukaziyo mikate yopereka nsembe yopangidwa m’chifanizo chake kuti tipereke kwa iye nsembe zachakumwazo?”+

20 Poyankha, Yeremiya anauza anthu onse amene anali kumuyankha ndi mawu amenewa, amuna amphamvu, akazi awo ndi anthu ena onse, kuti: 21 “Kodi Yehova sanakumbukire nsembe zautsi zimene munali kufukiza m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu?+ Kodi nsembe zimene inuyo,+ makolo anu,+ mafumu anu,+ akalonga anu+ ndi anthu a m’dzikolo anali kupereka, sizinalowe mumtima mwake?+ 22 Kenako Yehova sanathenso kupirira zimenezo chifukwa zochita zanu zinaipa kwambiri, chifukwa munachita zinthu zonyansa.+ Chotero dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chodabwitsa ndi chotembereredwa ndipo tsopano mulibe munthu wokhalamo.+ 23 Popeza munachimwira Yehova,+ munali kupereka nsembe zautsi+ ndipo simunamvere mawu a Yehova+ ndi kutsatira malamulo ake,+ malangizo ake ndi zikumbutso zake, n’chifukwa chake masoka onsewa akugwerani lero.”+

24 Ndiyeno Yeremiya anapitiriza kuuza anthu onse ndi akazi onse kuti: “Tamverani mawu a Yehova inu nonse a ku Yuda amene muli ku Iguputo kuno.+ 25 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Mawu awa akukhudza amuna inu ndi akazi anu.+ Akazi inu mumalankhula ndi pakamwa panu (ndipo anthu nonsenu mwakwaniritsa zonena zanu ndi manja anu) kuti: “Ife tidzakwaniritsa malonjezo athu+ akuti ‘tidzapereka nsembe zautsi kwa ‘mfumukazi yakumwamba’+ ndi kuti tidzapereka nsembe yachakumwa kwa iye.”+ Akazi inu mudzachitadi zimene mwalonjeza ndipo mudzakwaniritsadi malonjezo anu.’

26 “Tsopano imvani mawu a Yehova, inu nonse a ku Yuda amene mukukhala mu Iguputo muno.+ Yehova wanena kuti: “Ine ndalumbira m’dzina langa+ kuti m’dziko lonse la Iguputo simudzapezeka munthu aliyense wa ku Yuda woitanira pa dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Ambuye Wamkulu Koposa!’+ 27 Ine ndikhala tcheru kuti ndiwabweretsere tsoka osati zabwino.+ Ndipo anthu onse a ku Yuda amene ali m’dziko la Iguputo adzafa ndi lupanga ndi njala yaikulu kufikira atatheratu.+ 28 Anthu amene adzathawa lupanga kuchoka ku Iguputo kubwerera kudziko la Yuda adzakhala ochepa.+ Ndipo otsala onse ochokera ku Yuda amene akubwera m’dziko la Iguputo kuti adzakhalemo monga alendo adzadziwa kuti ndi mawu a ndani amene ali oona, mawu anga kapena mawu awo.”’”+

29 “Yehova wanena kuti: ‘Tsopano chizindikiro cha zimenezi kwa inu ndi ichi,+ ine ndikulangani m’dziko lino kuti mudziwe kuti mawu anga adzakwaniritsidwadi moti ndidzakugwetserani tsoka.+ 30 Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka Farao Hofira, mfumu ya Iguputo,+ m’manja mwa adani ake ndiponso m’manja mwa ofuna moyo wake,+ monga mmene ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mdani wa Zedekiyayo amene akufunanso moyo wake.”’”+

45 Mneneri Yeremiya analankhula ndi Baruki+ mwana wa Neriya pa nthawi imene Barukiyo anali kulemba mawu a Yeremiya m’buku.+ Chimenechi chinali chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Yeremiyayo anati:

2 “Ponena za iwe Baruki, Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, 3 ‘Iwe wanena kuti: “Tsoka ine!+ pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zopweteka zanga. Ndatopa ndi kuusa moyo* kwanga ndipo malo ampumulo sindikuwapeza.”’+

4 “Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndichita zimenezi m’dziko lonse.+ 5 Koma iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu.+ Leka kuzifunafuna.”’+

“‘Anthu onse ndikuwagwetsera tsoka+ ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako kulikonse kumene ungapite,’ watero Yehova.”+

46 Yehova anauza mneneri Yeremiya uthenga wokhudza mitundu ya anthu.+ 2 Uthenga umenewu unali wopita ku Iguputo+ ndipo unali kukhudza gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya Iguputo,+ amene anali kumtsinje wa Firate ku Karikemisi.+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo anagonjetsa mfumu imeneyi m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Uthengawo unali wakuti: 3 “Amuna inu, tengani zishango zanu zazikulu ndi zazing’ono ndipo konzekerani kumenya nkhondo.+ 4 Inu asilikali okwera pamahatchi, mangani mahatchi anu ndi kukwerapo, ndipo muvale zisoti zanu ndi kukhala okonzeka. Pukutani mikondo yanu ing’onoing’ono. Valani zovala zanu zamamba achitsulo.+

5 “‘N’chifukwa chiyani akuoneka kuti agwidwa ndi mantha? Akubwerera, ndipo amuna awo amphamvu aphwanyika ndi kukhala zidutswazidutswa. Iwo athawadi ndipo sanacheuke.+ Zochititsa mantha zili paliponse,’+ watero Yehova. 6 ‘Munthu waliwiro ndi munthu wamphamvu asayese dala kuthawa.+ Iwo apunthwa ndi kugwa.+ Zimenezi zachitikira kumpoto+ m’mphepete mwa mtsinje wa Firate.’

7 “Ndani uyu amene akubwera ngati mtsinje wa Nailo, kapena ngati mitsinje ya madzi ambiri amene akuwinduka?+ 8 Dziko la Iguputo likubwera ngati mtsinje wa Nailo,+ ndipo likubwera ngati madzi owinduka a m’mitsinje.+ Dzikolo likunena kuti, ‘Ndipita ndipo ndiphimba dziko lapansi. Ndiwononga mzinda ndi onse okhala mumzindawo.’+ 9 Inu mahatchi pitani. Inu magaleta thamangani ndi liwiro lalikulu! Lolani amuna amphamvu kuti apite. Lolani Kusi+ ndi Puti+ amene amadziwa kugwiritsira ntchito chishango kuti apite. Lolaninso Aludi+ amene amadziwa kukunga ndi kuponya uta kuti apite.

10 “Limeneli ndi tsiku la Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa ndipo ndi tsiku lobwezera chilango kwa adani ake.+ Lupanga lidzadya adaniwo ndi kukhuta ndipo lidzamwa magazi awo kufikira litathetsa ludzu lake. Lidzatero pakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi nsembe imene akufuna kupereka+ m’dziko la kumpoto, m’mphepete mwa mtsinje wa Firate.+

11 “Iwe namwali, mwana wamkazi wa Iguputo,+ pita ku Giliyadi kuti ukatenge mafuta a basamu.+ Wachulukitsa njira zochiritsira zosathandiza koma sudzachiritsidwa.+ 12 Mitundu ya anthu yamva zochititsa manyazi zimene zakuchitikira+ ndipo kulira kwako kwamveka m’dziko lonse.+ Amuna amphamvu apunthwitsana ndi kugwetsana.+ Onse agwera limodzi.”

13 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza kubwera kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo kudzaukira dziko la Iguputo.+ Iye anati: 14 “Nenani zimenezi mu Iguputo amuna inu. Lengezani zimenezi ku Migidoli,+ ku Nofi+ ndi ku Tahapanesi.+ Nenani kuti, ‘Imani chilili. Konzekani.+ Pakuti lupanga lidzawononga chilichonse chokuzungulirani.+ 15 N’chifukwa chiyani anthu anu amphamvu akokoloka?+ Iwo sanachirimike pakuti Yehova wawathamangitsa.+ 16 Ambiri mwa iwo akupunthwa ndi kugwa. Ndipo akuuzana kuti: “Imirira, tiye tibwerere kwa anthu a mtundu wathu ndi kudziko la abale athu chifukwa takumana ndi lupanga loopsa.”’ 17 Kumeneko asilikali anu akunena kuti, ‘Farao mfumu ya Iguputo akungoopseza ndi pakamwa chabe.+ Iye wathetsa nthawi ya chikondwerero.’+

18 “‘Pali ine Mulungu wamoyo, Nebukadirezara adzabwera ndi kuonekera ngati phiri la Tabori+ pakati pa mapiri ena, ndiponso ngati phiri la Karimeli+ m’mphepete mwa nyanja,’ yatero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ 19 ‘Longedza katundu wopita naye ku ukapolo,+ iwe mwana wamkazi wokhala+ mu Iguputo. Pakuti mzinda wa Nofi+ udzakhala chinthu chodabwitsa ndipo adzautentha, moti simudzapezeka aliyense wokhalamo.+ 20 Iguputo ndi ng’ombe yaikazi yokongola kwambiri imene sinaberekepo. Udzudzu wovutitsa ndi wowononga wochokera kumpoto udzabwera kuti umuwononge.+ 21 Kuwonjezera apo, asilikali amene wawalemba ganyu ali ngati ana a ng’ombe onenepa,+ koma iwonso agonja+ ndipo onse athawa. Sanathe kulimba+ pakuti tsiku lawo la tsoka ndiponso nthawi ya kulangidwa kwawo yafika.’+

22 “‘Mawu ake ali ngati mawu a njoka imene ikuthawa.+ Pakuti adani adzafika mwamphamvu ndipo adzabwera kwa iye ali ndi nkhwangwa ngati anthu otola nkhuni.* 23 Adaniwo ndi ochuluka kwambiri kuposa dzombe+ ndipo ndi osawerengeka, moti adzadula nkhalango+ yake chifukwa sangathe kudutsamo,’ watero Yehova. 24 ‘Mwana wamkazi+ wa Iguputo adzachitadi manyazi, ndipo adzaperekedwa m’manja mwa anthu a kumpoto.’+

25 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndilanga Amoni+ wa ku No,+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake+ ndi mafumu ake.+ Ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+

26 “‘Ndidzapereka anthu a ku Iguputo m’manja mwa anthu amene akufuna moyo wawo, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ ndi m’manja mwa atumiki ake. Kenako anthu adzakhalanso m’dzikolo monga mmene zinalili kale,’+ watero Yehova.

27 “‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope ndipo usagwidwe ndi mantha, iwe Isiraeli.+ Pakuti ine tsopano ndikukupulumutsa kuchokera kutali. Mbewu yako ndikuipulumutsa kuchokera m’dziko limene iwo anali akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndi kukhala mwabata ndiponso mosatekeseka, popanda womuopsa.+ 28 Chotero, iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, pakuti ine ndili ndi iwe.+ Ine ndidzafafaniza mitundu yonse ya anthu kumene ndakubalalitsirako,+ koma iwe sindidzakufafaniza.+ Ngakhale zili choncho, ndidzakulanga pamlingo woyenera,+ ndipo ndithu sindidzakusiya osakulanga,’+ watero Yehova.”

47 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti.+ Pa nthawiyi, Farao anali asanathire nkhondo mzinda wa Gaza.+ 2 Yehova anati:

“Taonani! Madzi akubwera+ kuchokera kumpoto+ ndipo madzi ake ndi achigumula. Adzamiza dziko ndi zonse zokhala mmenemo.+ Adzamizanso mzinda ndi zonse zokhala mmenemo. Amuna adzalira mokuwa, ndipo aliyense wokhala m’dzikolo adzalira mofuula.+ 3 Abambo adzathawa osayang’ana m’mbuyo kuti apulumutse ana awo. Adzachita izi chifukwa chakuti sadzalimba mtima pakumva mgugu wa mahatchi ake,+ phokoso la magaleta ake ankhondo+ ndi kulira kwa mawilo ake.+ 4 Iwo adzachita mantha chifukwa cha tsiku limene likubwera. Tsikuli ndi lofunkha zinthu za Afilisiti+ onse ndi kupha wopulumuka aliyense wothandiza+ Turo+ ndi Sidoni.+ Pakuti Yehova adzafunkha zinthu za Afilisiti+ amene atsala ochokera pachilumba cha Kafitori.+ 5 Gaza+ adzameta mpala+ chifukwa cha chisoni. Asikeloni+ amuwononga ndi kumukhalitsa chete. Inu otsala a m’chigwa cha Gaza ndi Asikeloni, mudzadzichekacheka kufikira liti?+

6 “Eyaa! iwe lupanga la Yehova.+ Kodi sukhala chete kufikira liti? Bwerera m’chimake.+ Pumula, ndipo ukhale chete.

7 “Kodi lupangali lingakhale chete bwanji pamene Yehova ndi amene walilamula? Liyenera kupita ku Asikeloni ndi m’mphepete mwa nyanja.+ Iye walituma kuti likakhale kumeneko.”

48 Ponena za Mowabu+ Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti:+ “Tsoka Nebo+ chifukwa wafunkhidwa! Mzinda wa Kiriyataimu+ walandidwa ndipo anthu ake achita manyazi. Anthu okhala m’malo okwezeka achitetezo achita manyazi ndipo achita mantha.+ 2 Mowabu sakutamandidwanso.+ Anthu a ku Hesiboni+ amukonzera chiwembu ndipo akunena kuti: ‘Bwerani amuna inu, tiyeni tifafanize Mowabu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’+

“Inunso anthu a ku Madimeni khalani chete. Lupanga likukutsatirani. 3 Ku Horonaimu+ kwamveka kulira kofuula, kufunkha ndi chiwonongeko chachikulu. 4 Mowabu wawonongeka.+ Kulira kwa ana ake kwamveka. 5 Anthu akupita ku Luhiti+ akulira. Akupita akulira kwambiri. Amene akutsika kuchokera ku Horonaimu akufuula mowawidwa mtima chifukwa amva za chiwonongeko.+

6 “Thawani. Pulumutsani moyo wanu+ ndipo mukhale ngati mtengo umene uli wokhawokha m’chipululu.+ 7 Inu mudzagwidwa ndi adani chifukwa mukudalira ntchito zanu ndi chuma chanu.+ Kemosi+ adzatengedwa kupita ku ukapolo+ pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.+ 8 Wofunkha adzalowa mumzinda uliwonse+ ndipo sipadzapezeka mzinda wopulumuka.+ Zigwa ndi malo athyathyathya adzawonongedwa ndithu, izi ndi zimene Yehova wanena.

9 “Anthu inu perekani chizindikiro cha pamsewu kwa anthu a ku Mowabu pakuti adzachoka pamene dziko lawo likusanduka bwinja.+ Mizinda yake idzasanduka chinthu chodabwitsa ndipo simudzapezeka aliyense wokhalamo.+

10 “Wotembereredwa ndi munthu wozengereza kugwira ntchito imene Yehova wamupatsa.+ Wotembereredwa ndi munthu wopewa kukhetsa magazi ndi lupanga lake.

11 “Anthu a ku Mowabu akhala mosatekeseka kuyambira pa unyamata wawo+ ndipo akukhalabe mosatekeseka ngati vinyo wansenga.+ Iwo sanatsanulidwepo kuchoka m’chiwiya china kupita m’chiwiya china ndipo sanapitepo ku ukapolo. N’chifukwa chake kukoma kwawo sikunawonjezeke ndipo fungo lawo silinasinthe.

12 “‘Choncho masiku adzafika,’ watero Yehova, ‘ndipo ndidzawatumizira anthu opendeketsa mitsuko ndipo adzawapendeketsa.+ Iwo adzawatsanula m’ziwiya zawo ndipo adzaswa mitsuko yawo ikuluikulu kukhala mapalemapale. 13 Amowabuwo adzachita manyazi ndi Kemosi,+ monga mmene anthu a m’nyumba ya Isiraeli achitira manyazi ndi Beteli, mzinda umene anali kuudalira.+ 14 N’chifukwa chiyani anthu inu mukunena kuti: “Ndife amuna amphamvu+ ndi anyonga oyenera kumenya nkhondo”?’

15 “‘Mowabu wafunkhidwa, ndipo munthu wina adzaukira mizinda yake.+ Anyamata osankhidwa a m’mizindayo apita kokaphedwa,’+ yatero Mfumu imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+

16 “Tsoka la Amowabu lili pafupi, ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ 17 Onse owazungulira, onse odziwa dzina lawo adzawamvera chisoni.+ Anthu inu nenani kuti, ‘Ndodo yamphamvu ndiponso yokongola yathyoka!’+

18 “Tsika pamalo ako aulemerero ndipo ukhale ndi ludzu, iwe mwana wamkazi wokhala+ ku Diboni+ chifukwa wowononga Mowabu wabwera kudzakuukira. Iye adzasandutsa bwinja malo ako a mipanda yolimba kwambiri.+

19 “Ima chilili ndi kuona zimene zikuchitika m’njira, iwe mkazi wokhala ku Aroweli.+ Funsa mwamuna ndi mkazi amene akuthawa. Uwafunse kuti, ‘Chachitika n’chiyani?’+ 20 Anthu a ku Mowabu achita manyazi pakuti agwidwa ndi mantha aakulu.+ Lirani mofuula. Amuna inu, lengezani ku Arinoni+ kuti Mowabu wafunkhidwa. 21 Chiweruzo chafika padziko lathyathyathya.+ Chafika ku Holoni, Yahazi,+ Mefaata,+ 22 Diboni,+ Nebo,+ Beti-dibilataimu, 23 Kiriyataimu,+ Beti-gamuli, Beti-meoni,+ 24 Kerioti,+ Bozira+ ndi mizinda yonse ya m’dziko la Mowabu, yakutali ndi yapafupi.

25 “‘Nyanga* ya Mowabu yadulidwa+ ndipo dzanja lake lathyoledwa,’+ watero Yehova. 26 ‘Muledzeretseni+ anthu inu chifukwa wadzikuza pamaso pa Yehova.+ Mowabu wadzigwetsa ndipo wagubuduka m’masanzi ake,+ ndipo wakhaladi chinthu chotonzedwa.

27 “‘Kodi Isiraeli sanasanduke chinthu chotonzedwa kwa inu?+ Kapena kodi anapezeka pakati pa mbala zenizeni?+ Inu munali kupukusa mitu moipidwa pamene munali kumunenera zinthu zoipa.

28 “‘Inu anthu okhala ku Mowabu, chokani mumzinda ndi kukakhala pathanthwe.+ Khalani ngati njiwa imene imamanga chisa chake pakhomo la dzenje m’matanthwemo.’”+

29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu.+ Iye ndi wodzikuza kwambiri. Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, kudzikuza kwake ndi kudzitukumula kwa mtima wake.”+

30 “‘Ine ndadziwa za mkwiyo wake,’ watero Yehova, ‘ndipo kudzikuza kwakeko sikudzaphula kanthu.+ Iye sadzachita zonena zake zopanda pakezo.+ 31 N’chifukwa chake Mowabu ndidzamukuwira, ndipo ndidzafuulira Mowabu yense.+ Anthu adzalirira amuna a ku Kiri-haresi.+

32 “‘Iwe mtengo wa mpesa wa ku Sibima+ ndidzakulirira kuposa mmene ndingalirire Yazeri.+ Mphukira zako zosangalala zawoloka nyanja. Zafika kunyanja, ku Yazeri.+ Munthu wofunkha waukira zipatso zako za m’chilimwe*+ ndi mphesa zimene wakolola.+ 33 Kusangalala ndi kukondwera zachotsedwa m’munda wa zipatso ndiponso m’dziko la Mowabu.+ Ndachititsa kuti vinyo asapezeke moponderamo mphesa.+ Palibe amene adzapondaponda mphesa akufuula mosangalala. Padzamveka kufuula koma osati kwachisangalalo.’”+

34 “‘Kulira kochokera ku Hesiboni+ kudzamveka ku Eleyale+ ndi ku Yahazi.+ Kulira kochokera ku Zowari+ kudzamveka ku Horonaimu+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Madzi a ku Nimurimu+ nawonso adzawonongedwa. 35 Ndidzachititsa kuti m’dziko la Mowabu musapezeke aliyense wobweretsa nsembe kumalo okwezeka komanso wofukiza nsembe yautsi kwa mulungu wake,’+ watero Yehova. 36 ‘Choncho mtima wanga udzachitira Mowabu phokoso ngati zitoliro.+ Mtima wanga udzachitira phokoso amuna a ku Kiri-haresi+ ngati zitoliro. Chotero zinthu zochuluka zimene wapanga zidzawonongeka.+ 37 Mutu uliwonse wametedwa mpala,+ ndipo ndevu zonse n’zometa.+ M’manja monse ndi mochekekachekeka,+ ndipo anthu onse amanga ziguduli m’chiuno mwawo.’”+

38 “‘Anthu akulira pamadenga onse a nyumba za ku Mowabu ndi m’mabwalo ake onse.+ Akulira chifukwa ndaphwanya Mowabu ngati chiwiya chimene sichikundikondweretsa,’+ watero Yehova. 39 ‘Mowabu wachita mantha. Lirani mofuula anthu inu! Mowabu watembenuka ndipo wachita manyazi.+ Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka ndi chochititsa mantha kwa onse omuzungulira.’”

40 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani! Monga mmene chiwombankhanga chimatsikira ndi kugwira chakudya chake,+ wina adzatambasula mapiko ake ndi kugwira Mowabu.+ 41 Matauni adzalandidwa. Malo ake odalirika adzalandidwa. Pa tsikulo, mitima ya amuna amphamvu a ku Mowabu idzakhala ngati mtima wa mkazi amene akumva zowawa za pobereka.’”+

42 “‘Mowabu adzawonongedwa ndipo sadzakhalanso mtundu wa anthu+ chifukwa wadzikweza pamaso pa Yehova.+ 43 Mantha, dzenje ndi msampha zili pa iwe munthu wokhala ku Mowabu,’+ watero Yehova. 44 ‘Aliyense wothawa chifukwa cha mantha adzagwera m’dzenje. Aliyense wotuluka m’dzenjemo adzagwidwa mumsampha.’+

“‘Pakuti ine ndidzachititsa kuti chaka chopereka chilango kwa anthu a ku Mowabu chifike,’+ watero Yehova. 45 ‘Anthu othawa aima chilili mumthunzi wa Hesiboni ndipo alibe mphamvu. Moto udzachokera ku Hesiboni+ ndipo malawi a moto adzachokera ku Sihoni+ ndi kutentha Mowabu m’mutu, m’mphepete mwa makutu, komanso paliwombo pa ana osokoneza.’+

46 “‘Tsoka iwe Mowabu!+ Anthu a Kemosi+ awonongedwa. Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina. 47 M’masiku otsiriza ndidzasonkhanitsa Amowabu onse amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’+ watero Yehova. ‘Apa ndi pamene pathera ziweruzo za Mowabu.’”+

49 Ponena za ana a Amoni+ Yehova wanena kuti: “Kodi Isiraeli alibe ana aamuna, kapena kodi alibe wolandira cholowa? N’chifukwa chiyani Malikamu+ watenga Gadi+ kukhala cholowa chake? N’chifukwa chiyani anthu olambira Malikamu akukhala m’mizinda ya Isiraeli?”+

2 “‘Choncho taonani! Masiku adzafika,’ watero Yehova, ‘ndipo Raba,+ umene ndi mzinda wa ana a Amoni, ndidzaulizira chizindikiro chakuti kukubwera nkhondo.+ Ndipo mzindawu udzasanduka bwinja ndi mulu wadothi.+ Midzi yake yozungulira+ idzatenthedwa.’+

“‘Isiraeli adzatenga dziko la anthu amene analanda dziko lake,’+ watero Yehova.

3 “‘Fuula+ iwe Hesiboni+ pakuti mzinda wa Ai wafunkhidwa zinthu zake! Lirani inu midzi yozungulira Raba. Valani ziguduli.+ Lirani mokuwa ndi kuyendayenda m’makola amiyala chifukwa Malikamu adzatengedwa kupita ku ukapolo+ pamodzi ndi ansembe ndi akalonga ake onse.+ 4 Bwanji umadzitama chifukwa cha zigwa zako, zigwa zoyenda madzi,+ iwe mwana wamkazi wosakhulupirika? Iwe ukudalira chuma chako,+ ponena kuti: “Ndani angabwere kwa ine?”’”+

5 “Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa+ wanena kuti, ‘Ine ndikukubweretsera chinthu chochititsa mantha+ kuchokera kwa anthu onse okuzungulira. Ndiponso anthu inu mudzabalalitsidwa, aliyense kulowera kwake,+ ndipo sipadzapezeka wosonkhanitsa pamodzi anthu othawawo.’”

6 “‘Pambuyo pake ndidzasonkhanitsa ana a Amoni+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’ watero Yehova.”

7 Ponena za Edomu, Yehova wa makamu wanena kuti: “Kodi nzeru+ zinatha ku Temani?+ Kodi anthu ozindikira sakuperekanso malangizo anzeru? Kodi nzeru zawo zavunda?+ 8 Thawani!+ Bwererani! Pitani kumalo otsika kuti mukakhale kumeneko,+ inu okhala ku Dedani!+ Pakuti Esau ndidzamugwetsera tsoka pa nthawi yomulanga.+ 9 Kodi okolola mphesa atabwera kwa iwe sadzasiyako zina zoti ena akunkhe? Ndipotu akuba atakubwerera usiku, adzangowononga zokhazo zimene akufuna.+ 10 Koma ine ndidzawononga zinthu zonse za Esau ndi kumusiya alibiretu kalikonse.+ Ndidzavundukula malo ake obisika+ moti munthu sadzatha kubisala.+ Mbadwa zake, abale ake ndi anthu oyandikana naye adzafunkhidwa,+ ndipo Esau sadzakhalaponso.+ 11 Asiyeni ana anu amasiye.*+ Ine ndidzawasiya amoyo ndipo akazi anu amasiye adzandikhulupirira.”+

12 Yehova wanena kuti: “Taonani! Ngakhale kuti sanazolowere kumwa za m’kapu, iwo adzamwa ndithu.+ Kodi iwe udzasiyidwa osapatsidwa chilango? Ayi, sudzasiyidwa osapatsidwa chilango pakuti udzamwa ndithu za m’kapumo.”+

13 “Ine ndalumbira pa dzina langa+ kuti Bozira+ adzakhala chinthu chodabwitsa, chotonzedwa ndiponso malo owonongedwa.+ Iye adzakhala wotembereredwa ndipo mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka kalekale,”+ watero Yehova.

14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti: “Sonkhanani, muukireni ndi kumuthira nkhondo.”+

15 “Taona! Ndakuchepetsa pakati pa mitundu ina, ndipo ndakupeputsa pakati pa anthu.+ 16 Iwe unachititsa anthu kunjenjemera ndiponso unali ndi mtima wodzikuza,+ koma zimenezi zakunyenga, iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe pamwamba pa phiri. Ngakhale kuti umamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga+ ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,”+ watero Yehova. 17 “Edomu adzakhala chinthu chodabwitsa.+ Aliyense wodutsa pafupi naye adzamuyang’anitsitsa modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yonse imene idzamugwera.+ 18 Monga mmene Sodomu ndi Gomora pamodzi ndi midzi yapafupi inawonongedwera,+ Edomu adzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso m’dzikolo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova.

19 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango+ kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano. Iye adzafika pamalo otetezeka+ odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzamuthamangitsa pamalowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo, pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+ 20 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha kuchitira Edomu+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire anthu okhala ku Temani:+ Ndithudi, chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku, ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+ 21 Dziko lapansi layamba kugwedezeka chifukwa cha mkokomo wa kugwa kwawo.+ Kukumveka kulira!+ Kulirako kwamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.+ 22 Taonani! Wina adzakwera kenako n’kutsika ngati chiwombankhanga chimene chikufuna kugwira chakudya chake.+ Adzatambasulira mapiko ake pa Bozira,+ ndipo pa tsikulo mtima wa amuna amphamvu a ku Edomu udzakhala ngati mtima wa mkazi amene akumva zowawa za pobereka.”+

23 Uthenga wokhudza Damasiko+ ndi wonena kuti: “Hamati+ ndi Aripadi+ achita manyazi chifukwa chakuti amva uthenga woipa. Iwo apasuka+ ndipo nyanja yawinduka, moti singathe kukhala bata.+ 24 Damasiko wachita mantha. Watembenuka ndi kuthawa ndipo wapanikizika.+ Iye wagwidwa ndi nkhawa ndiponso zowawa za pobereka ngati zimene zimagwira mkazi amene akubereka.+ 25 Kodi zatheka bwanji kuti anthu asachoke mumzinda wotamandika, mudzi wobweretsa chisangalalo?+

26 “Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo ake, ndipo amuna ake ankhondo adzawakhalitsa chete pa tsiku limenelo,”+ watero Yehova wa makamu. 27 “Mipanda ya Damasiko ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzatentha nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.”+

28 Ponena za Kedara+ ndi maufumu a Hazori+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anawapha,+ Yehova wanena kuti: “Nyamukani amuna inu, pitani ku Kedara ndipo mukafunkhe zinthu za ana a Kum’mawa.+ 29 Mahema awo,+ nkhosa zawo,+ nsalu za mahema awo ndi zinthu zawo zonse zidzatengedwa.+ Ngamila zawo+ zidzalandidwa. Anthu adzawalirira kuti, ‘Zochititsa mantha zili paliponse!’”+

30 “Thawani, thawirani kutali. Tsikirani kumalo akuya kuti mukakhale kumeneko, inu okhala ku Hazori,”+ watero Yehova. “Pakuti Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ waganiza zokuukirani ndi kukuchitirani zoipa.”

31 “Nyamukani, amuna inu. Pitani kukaukira mtundu wa anthu umene ukukhala mosatekeseka+ ndi mwamtendere!”+ watero Yehova.

“Kumeneko kulibe zitseko ndi mipiringidzo. Anthu ake amakhala kwaokhaokha.+ 32 Ngamila zawo+ zidzafunkhidwa ndipo ziweto zawo zochulukazo zidzawonongedwa. Anthu amene amadulira ndevu zawo za m’mbali+ ndidzawabalalitsira kumbali zonse.*+ Ndidzawagwetsera tsoka kuchokera kumadera onse owazungulira,” watero Yehova. 33 “Hazori+ adzakhala malo obisalamo mimbulu+ ndipo adzakhala bwinja mpaka kalekale. Palibe munthu amene adzakhala kumeneko, moti mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo.”+

34 Yehova anauza Yeremiya mawu okhudza Elamu+ kuchiyambi kwa ufumu wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, kuti: 35 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndikuthyola uta wa Aelamu,+ umene ndiwo mphamvu yawo yaikulu. 36 Anthu a ku Elamu ndidzawabweretsera mphepo zinayi kuchokera kumalekezero anayi a kumwamba.+ Ndidzawabalalitsira kumphepo zonsezi+ ndipo sipadzapezeka mtundu wa anthu kumene obalalitsidwa+ a Elamu sadzapitako.’”

37 “Aelamu ndidzawachititsa mantha pamaso pa adani awo ndi pamaso pa anthu amene akufunafuna moyo wawo. Ndidzawabweretsera tsoka, mkwiyo wanga woyaka moto,”+ watero Yehova. “Ndidzawatumizira lupanga kufikira nditawafafaniza.”+

38 “Ndidzaika mpando wanga wachifumu ku Elamu,+ ndipo kumeneko ndidzawononga ndi kuchotsa mfumu ndi akalonga,” watero Yehova.

39 “Ndiyeno m’masiku otsiriza+ ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a ku Elamu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,”+ watero Yehova.

50 Yehova ananena mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi,+ kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati: 2 “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina.+ Imikani mtengo wachizindikiro+ ndipo lengezani zimenezi. Musabise kalikonse amuna inu. Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+ Beli wachititsidwa manyazi.+ Merodake wachita mantha. Mafano a Babulo achita manyazi.+ Mafano ake onyansawo* achita mantha.’ 3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+

4 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo+ ana a Isiraeli pamodzi ndi ana a Yuda adzabwera,”+ watero Yehova. “Iwo adzayenda akulira+ ndipo adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+ 5 Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayang’ana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tidziphatike kwa Yehova mwa kuchita pangano lokhalapo mpaka kalekale limene silidzaiwalika.’+ 6 Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosakazidwa.+ Abusa awo awayendetsa uku ndi uku.+ Awayendetsa uku ndi uku m’mapiri popanda cholinga.+ Awachotsa paphiri ndi chitunda china kupita paphiri ndi chitunda china. Iwo aiwala malo awo ampumulo.+ 7 Anthu anga adyedwa ndi aliyense wowapeza,+ ndipo adani awo anena kuti,+ ‘Sitipalamula mlandu uliwonse, chifukwa iwo achimwira Yehova,+ malo okhalamo chilungamo.+ Achimwira Yehova chiyembekezo cha makolo awo.’”+

8 “Thawani m’Babulo ndipo tulukani m’dziko la Akasidi.+ Mukhale ngati mbuzi zamphongo ndi nkhosa zamphongo zimene zikutsogolera gulu lonse.+ 9 Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+ 10 Dziko la Kasidi lidzatengedwa monga zofunkha.+ Onse ofunkha zinthu zake adzakhutira,”+ watero Yehova.

11 “Anthu inu munali kusangalala,+ ndipo munali kukondwera pamene munali kulanda cholowa changa.+ Munali kudumphadumpha pamsipu ngati ng’ombe yaikazi yosaberekapo+ ndipo munali kulira ngati mahatchi amphongo.+ 12 Mayi wa anthu inu wachita manyazi kwambiri.+ Mayi amene anakuberekani wakhumudwa kwambiri.+ Taonani! Iye ndi wosafunika kwenikweni pakati pa mitundu ina, wakhala ngati dera lopanda madzi ndiponso chipululu.+ 13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, m’dzikomo simudzakhalanso anthu+ ndipo dziko lonselo lidzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi Babulo adzayang’ana modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+

14 “Zungulirani Babulo ndi kumuukira kuchokera kumbali zonse,+ inu nonse odziwa kukunga uta.+ Mulaseni+ ndipo musasunge muvi uliwonse, pakuti iye wachimwira Yehova.+ 15 Mufuulireni mfuu yankhondo kuchokera kumbali zonse.+ Wagwetsa manja ake+ ndipo zipilala zake zagwa. Mipanda yake yagwetsedwa,+ pakuti Yehova akumubwezera.+ Mubwezereni, ndipo monga mmene iye anachitira, inunso muchitireni zomwezo.+ 16 Iphani munthu wofesa mbewu mu Babulo,+ ndiponso amene akugwira chikwakwa nthawi yokolola. Aliyense adzabwerera kwa anthu a mtundu wake, ndipo aliyense adzathawira kudziko lakwawo chifukwa choopa lupanga loopsa.+

17 “Isiraeli ndi nkhosa yosochera.+ Mikango ndi imene yamuchititsa kuthawa.+ Poyamba, mfumu ya Asuri inadya Isiraeli,+ ndipo ulendo uno Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo yakukuta mafupa ake.+ 18 Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndikulanga mfumu ya Babulo ndi dziko lake ngati mmene ndinalangira mfumu ya Asuri.+ 19 Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli+ ndi ku Basana.+ Iye adzakhutira m’madera amapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+

20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+

21 “Ukirani dziko la Merataimu. Liukireni+ ndipo muukirenso anthu a ku Pekodi.+ Apululeni ndi kuwawonongeratu. Chitani zonse zimene ndakulamulani,” watero Yehova.+ 22 “Mukumveka phokoso lankhondo m’dzikomo ndi kuwonongeka kwakukulu.+ 23 Taonani! Nyundo yophwanyira mitundu+ ya anthu padziko lonse lapansi yathyoledwa ndipo yawonongeka.+ Taonani! Babulo wakhala chinthu chodabwitsa pakati pa mitundu ina.+ 24 Iwe Babulo ndinakutchera msampha ndipo wakodwa koma iwe sunadziwe.+ Unapezeka ndi kugwidwa chifukwa unali kulimbana ndi Yehova.+

25 “Yehova watsegula nkhokwe yake ya zida ndipo akutulutsamo zida zake zodzudzulira mwamphamvu.+ Akutero chifukwa chakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi ntchito yoti achite m’dziko la Akasidi.+ 26 Lowani m’dziko lake kuchokera kudera lakutali.+ Tsegulani nkhokwe zake.+ Muunjikeni pamodzi ngati mmene anthu amaunjikira milu ya tirigu+ ndipo mumuwonongeretu.+ M’dzikomo musapezeke aliyense wotsala.+ 27 Iphani ng’ombe zake zonse zazing’ono zamphongo.+ Zonse zipite kokaphedwa.+ Tsoka kwa iwo, chifukwa tsiku lawo lafika. Nthawi yoti alangidwe yafika.+

28 “Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa komanso amene apulumuka m’dziko la Babulo+ kuti akanene ku Ziyoni za chilango chimene Yehova Mulungu wathu akubwezera.+ Iye akubwezera kuwonongedwa kwa kachisi wake.+

29 “Babulo muitanireni oponya mivi ndi uta, onse okunga uta.+ Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa.+ Mubwezereni zimene anachita.+ Muchitireni zonse zimene iye anachita.+ Iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova, pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+ 30 Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo a mizinda yake,+ ndipo tsiku limenelo amuna ake onse ankhondo adzaphedwa,”+ watero Yehova.

31 “Taona! Iwe Babulo Wodzikuza,+ ndikukuthira nkhondo,”+ watero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.+ “Pakuti tsiku lako lifika, nthawi imene ndiyenera kukulanga. 32 Pa tsiku limenelo Babulo Wodzikuza ameneyu adzapunthwa ndi kugwa+ ndipo sipadzapezeka wina womudzutsa.+ Mizinda imene iye amalamulira ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzawononganso madera onse ozungulira mizindayo.”+

33 Yehova wa makamu wanena kuti: “Ana a Isiraeli ndi ana a Yuda, onse akuponderezedwa. Anthu onse amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina akuwakakamira+ ndipo sakuwalola kubwerera kwawo.+ 34 Wowawombola ndi wamphamvu,+ dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo+ kuti apumitse dziko lawo+ ndiponso kusokoneza mtendere wa anthu okhala m’Babulo.”+

35 “Lupanga lidzawononga Akasidi,”+ watero Yehova, “lidzawononganso anthu okhala m’Babulo,+ akalonga ake+ ndi anthu ake anzeru.+ 36 Lupanga lidzawononga anthu olankhula zinthu zopanda pake.+ Anthu amenewo adzachita zinthu mopanda nzeru.+ Lupanga lidzawononga anthu amphamvu a m’Babulo,+ moti adzagwidwa ndi mantha.+ 37 Lupanga lidzawononga mahatchi awo,+ magaleta awo ankhondo ndi khamu lonse la anthu a mitundu yosiyanasiyana amene ali pakati pawo+ ndipo adzakhala ngati akazi.+ Lupanga lidzawononga chuma chake+ ndipo chidzafunkhidwa. 38 Madzi ake adzawonongedwa ndipo adzauma.+ Dziko limeneli ndi la zifaniziro zogoba,+ ndipo anthu ake amachita zinthu mosaganiza chifukwa cha masomphenya awo ochititsa mantha. 39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+

40 “Monga mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ pamodzi ndi midzi yake yapafupi,+ dzikolo lidzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso mmenemo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova.

41 “Taona! Mtundu wa anthu ukubwera kuchokera kumpoto. Mtundu wamphamvu+ ndi mafumu akuluakulu+ adzautsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 42 Iwo amadziwa kuponya mivi ndi uta komanso nthungo.+ Amenewo ndi anthu ankhanza ndipo sadzakumvera chifundo.+ Phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja yowinduka.+ Adzakwera pamahatchi+ ndi kukuzungulira mogwirizana n’cholinga choti akuthire nkhondo, iwe mwana wamkazi wa Babulo.+

43 “Mfumu ya Babulo yamva za iwo,+ ndipo yataya mtima ndi kulefuka.+ Ikuda nkhawa ndipo ikumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.+

44 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano.+ Iye adzafika pamalo otetezeka odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzathamangitsa eni malowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo,+ pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+ 45 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha+ kuchitira Babulo+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire dziko la Akasidi.+ Ndithudi chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku,+ ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+ 46 Dziko lapansi lidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kugwidwa kwa Babulo,+ ndipo kulira kudzamveka pakati pa mitundu ya anthu.”+

51 Yehova wanena kuti: “Babulo+ pamodzi ndi anthu okhala ku Lebi-kamai ndikuwautsira chimphepo chowononga.+ 2 Ine ndidzatumiza anthu opeta ku Babulo kuti akamupete ndi kusiya dziko lake lili lopanda kanthu.+ Pa tsiku la tsoka lake, anthuwo adzamuukira kuchokera kumbali zonse.+

3 “Munthu wodziwa kukunga uta musamulole kuchita zimenezo.+ Musamulole kunyamuka kuti amenye nkhondo atavala chovala chamamba achitsulo.

“Anthu inu musamvere chisoni anyamata ake.+ Wonongani gulu lake lonse la asilikali.+ 4 Muwaphe ndi kusiya mitembo yawo ili paliponse m’dziko la Akasidi.+ Muwasiye mutawabaya m’misewu ya m’dzikolo.+

5 “Pakuti Mulungu, Yehova wa makamu,+ sanasiye Isiraeli ndi Yuda+ kuti akhale mkazi wamasiye. Dziko la Akasidi lili ndi mlandu waukulu pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+

6 “Thawani ndi kutuluka m’Babulo+ ndipo aliyense apulumutse moyo wake.+ Musawonongeke chifukwa cha zolakwa zake.+ Ino ndi nthawi yoti Yehova amubwezere chilango.+ Mulungu abwezera Babulo mogwirizana ndi zochita zake.+ 7 Babulo wakhala kapu yagolide m’dzanja la Yehova+ ndipo waledzeretsa dziko lonse lapansi.+ Mitundu ya anthu yaledzera ndi vinyo wake.+ N’chifukwa chake mitundu ya anthu ikuchita zinthu zamisala.+ 8 Babulo wagwa mwadzidzidzi moti wasweka.+ Mulireni mofuula anthu inu.+ M’patseni mafuta a basamu kuti muthetse ululu wake,+ mwina achira.”

9 “Tinafuna kuchiritsa Babulo, koma iye sanachiritsike. Tiyeni timusiye anthu inu+ ndipo aliyense wa ife apite kudziko lakwawo.+ Pakuti chiweruzo chake chafika kumwamba ndipo chakwera kufika m’mitambo.+ 10 Yehova watichitira zinthu zachilungamo.+ Bwerani kuti tisimbe ntchito za Yehova Mulungu wathu mu Ziyoni.”+

11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+ 12 Kwezerani mpanda wa Babulo mtengo wa chizindikiro.+ Wonjezerani alonda+ ndipo ikani alondawo pamalo awo. Konzekeretsani omenya nkhondo mobisalira anzawo.+ Pakuti Yehova waganiza zoti achite ndipo adzachitira anthu okhala ku Babulo zimene wanena.”+

13 “Iwe mkazi wokhala pamadzi ambiri,+ wokhala ndi chuma chochuluka,+ mapeto ako afika ndipo nthawi yako+ yoti uzipanga phindu yatha.+ 14 Yehova wa makamu walumbira m’dzina lake+ kuti, ‘M’dziko lako ndidzadzazamo amuna ngati dzombe+ ndipo amunawo adzaimba mokondwa chifukwa chokugonjetsa.’+ 15 Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake,+ amene mwanzeru+ zake anakhazikitsa dziko+ limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.+ 16 Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo, ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake. 17 Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri aliyense wa zitsulo adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+ 18 Iwo ndi achabechabe,+ ntchito yoyenera kutonzedwa.+ Mulungu akadzatembenukira kwa iwo, adzawawononga.+

19 “Koma Mulungu wa Yakobo sali ngati mafanowa.+ Iye ndi amene anapanga china chilichonse.+ Mulungu ameneyu ndiye ndodo ya cholowa chake+ ndipo dzina lake ndi Yehova wa makamu.”+

20 “Iwe ndiwe chibonga changa, zida zanga zankhondo.+ Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mitundu ya anthu kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzawononga maufumu. 21 Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya hatchi ndi wokwerapo wake kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya magaleta* ankhondo ndi okweramo ake kukhala zidutswazidutswa.+ 22 Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mwamuna ndi mkazi kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mwamuna wachikulire ndi kamnyamata kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mnyamata ndi namwali kukhala zidutswazidutswa. 23 Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya m’busa ndi gulu lake la ziweto kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mlimi ndi ziweto zake zolimira kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri kukhala zidutswazidutswa. 24 Ndidzabwezera Babulo ndi anthu onse okhala m’dziko la Kasidi zoipa zonse zimene anachita ku Ziyoni anthu inu mukuona,”+ watero Yehova.

25 “Ine ndikuthira nkhondo iwe+ phiri lowononga,+ amene wawononga dziko lonse lapansi.+ Ndidzatambasula dzanja langa ndi kukuthira nkhondo. Ndidzakugubuduza kukuchotsa pamatanthwe ndipo ndidzakusandutsa phiri lotenthedwa ndi moto,” watero Yehova.+

26 “Anthu sadzatenga mwala kuchokera kwa iwe kuti ukakhale mwala wapakona kapena mwala wapamaziko+ chifukwa udzakhala mabwinja mpaka kalekale,”+ watero Yehova.

27 “Kwezani mtengo wa chizindikiro amuna inu.+ Imbani lipenga pakati pa mitundu ya anthu. Konzekeretsani+ mitundu ya anthu yoti imuthire nkhondo. Muitanireni maufumu a ku Ararati,+ ku Mini ndi ku Asikenazi.+ Muikireni wolemba anthu usilikali. Mubweretsereni mahatchi+ ngati dzombe lokhala ndi ubweya. 28 Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo, mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake, atsogoleri ake onse ndi madera onse olamulidwa ndi aliyense wa amenewa. 29 Dziko ligwedezeke ndi kumva ululu waukulu,+ chifukwa Yehova waganiza zokhaulitsa Babulo kuti dzikolo likhale chinthu chodabwitsa, lopanda munthu wokhalamo.+

30 “Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo. Iwo angokhala m’malo otetezeka. Mphamvu zawo zatha.+ Akhala ngati akazi.+ Nyumba za m’Babulo zatenthedwa. Mipiringidzo yake yathyoledwa.+

31 “Munthu mmodzi wothamanga wakumana ndi mnzake, ndipo mthenga mmodzi wakumana ndi mnzake,+ onsewa akukanena kwa mfumu ya Babulo kuti mzinda wake walandidwa kumbali zonse.+ 32 Akukanenanso kuti malo owolokera mtsinje alandidwa+ ndipo ngalawa zagumbwa* zatenthedwa. Amuna ankhondo nawonso asokonezeka.”+

33 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mwana wamkazi wa Babulo ali ngati malo opunthira mbewu.+ Ino ndi nthawi yomupondaponda. Koma kwatsala ka nthawi pang’ono kuti nthawi yokolola imufikire.”+

34 “Nebukadirezara mfumu ya Babulo wandidya.+ Wandisokoneza ndi kundisandutsa chiwiya chopanda kanthu. Wandimeza ngati chinjoka chachikulu.+ Wakhuta zinthu zanga zokoma ndipo wanditsukuluza. 35 Mkazi wokhala mu Ziyoni adzanena kuti, ‘Chiwawa chimene achitira ine ndi thupi langa chigwerenso Babulo.’+ Yerusalemu adzanena kuti, ‘Magazi anga akhale pa anthu okhala m’dziko la Kasidi.’”+

36 Choncho Yehova wanena kuti: “Ine ndikukuyankhira mlandu,+ ndipo ndidzakubwezerera chilango.+ Ndidzaphwetsa nyanja yake ndi zitsime zake.+ 37 Babulo adzakhala milu yamiyala+ ndi malo obisalamo mimbulu.+ Adzakhala chinthu chodabwitsa ndi chochiimbira mluzu ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+ 38 Anthu onse okhala mmenemo adzabangula ngati mikango yamphamvu. Adzalira ngati ana a mikango.”

39 “Chilakolako chawo chikadzakhala champhavu kwambiri ndidzawakonzera mapwando ndipo ndidzawaledzeretsa kuti asangalale.+ Pamenepo adzagona tulo tomwe tidzakhalapo mpaka kalekale, ndipo sadzadzukanso,”+ watero Yehova. 40 “Ndidzapita nawo kumalo owaphera ngati nkhosa zamphongo zopita kokaphedwa, ngati nkhosa zamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo.”+

41 “Taonani! Sesaki walandidwa.+ Dziko lotamandidwa padziko lonse lapansi latengedwa.+ Babulo wakhala chinthu chodabwitsa pakati pa mitundu ya anthu.+ 42 Nyanja yasefukira ndi kumiza Babulo. Mzinda wa Babulo wamizidwa pansi pa mafunde ambiri a nyanjayo.+ 43 Mizinda yake yakhala chinthu chodabwitsa, dziko lopanda madzi komanso chipululu.+ Mizindayo yakhala ngati dziko limene simukukhala munthu aliyense ndipo sipadzapezeka mwana aliyense wa munthu wodutsa mmenemo.+ 44 Ndidzalanga Beli+ ku Babulo ndipo ndidzamulavulitsa zimene wameza.+ Mitundu ya anthu sidzakhamukiranso kwa iye.+ Kuwonjezera apo, mpanda wa Babulo udzagwa.+

45 “Tulukani mwa iye anthu anga,+ ndipo aliyense wa inu apulumutse moyo wake+ ku mkwiyo wa Yehova woyaka moto.+ 46 Mukapanda kutero mudzaopa m’mitima yanu+ ndipo mudzachita mantha chifukwa cha uthenga umene udzamveka m’dzikolo. M’chaka chimodzi uthengawo udzafika, kenako m’chaka china mudzamvekanso uthenga ndipo padzachitika chiwawa padziko lapansi. Wolamulira adzaukira wolamulira mnzake. 47 Taonani! Masiku adzafika ndipo ndidzalanga zifaniziro zogoba za ku Babulo.+ Dziko lake lonse lidzachita manyazi ndipo mitembo ya anthu ake onse ophedwa idzakhala paliponse mumzindawo.+

48 “Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zidzafuula mosangalala chifukwa cha kugwa kwa Babulo,+ pakuti ofunkha zinthu zake adzafika kuchokera kumpoto,”+ watero Yehova. 49 “Babulo sanangophetsa anthu a mu Isiraeli okha+ koma anaphetsanso anthu a padziko lonse lapansi m’Babulomo.+

50 “Inu amene mwathawa lupanga, pitirizani kuthawa. Musaime chilili.+ Kumbukirani Yehova+ pamene muli kutali kwambiri ndipo mukumbukirenso Yerusalemu mumtima mwanu.”+

51 “Tamva mawu otonza+ ndipo tachita manyazi.+ Manyazi atiphimba nkhope+ chifukwa alendo aukira malo oyera m’nyumba ya Yehova.”+

52 “Chotero masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo ndidzalanga zifaniziro zake zogoba.+ M’dziko lake lonse anthu obayidwa adzakhala akubuula.”+

53 “Ngakhale Babulo atakwera kukafika kumwamba,+ kapenanso atakweza mphamvu zake kukhala zosafikirika,+ anthu ofunkha zinthu zake ochokera kwa ine adzamupeza,”+ watero Yehova.

54 “Tamverani! Ku Babulo kukumveka kulira kofuula+ ndipo m’dziko la Akasidi mukumveka phokoso la chiwonongeko chachikulu,+ 55 chifukwa Yehova akufunkha zinthu za Babulo ndi kuthetsa mawu ake aakulu.+ Mafunde awo adzachita phokoso ngati madzi ambiri.+ Komanso phokoso la mawu awo lidzamveka m’Babulo. 56 Wofunkha adzafikira Babulo+ ndipo amuna ake amphamvu adzagwidwa.+ Mauta awo adzathyoledwa,+ pakuti Yehova ndi Mulungu wobwezera.+ Iye adzawabwezera ndithu.+ 57 Ndidzaledzeretsa akalonga, anthu ake anzeru, abwanamkubwa ake, atsogoleri ake ndi anthu ake amphamvu.+ Adzagona tulo tomwe tidzakhalapo mpaka kalekale ndipo sadzadzukanso,”+ yatero Mfumu,+ imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+

58 Yehova wa makamu wanena kuti: “Ngakhale kuti mpanda wa Babulo ndi waukulu udzagwetsedwa ndithu.+ Ngakhale kuti zipata zake ndi zazitali zidzatenthedwa.+ Anthu adzagwira ntchito yolemetsa pachabe.+ Mitundu ya anthu idzagwira ntchito yolemetsa imene idzawonongedwa ndi moto+ ndipo adzangodzitopetsa.”

59 Mneneri Yeremiya anapereka malangizo kwa Seraya mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya.+ Anapereka malangizowo pamene Seraya anapita ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo m’chaka chachinayi cha ufumu wake. Pa nthawiyo Seraya anali mkulu woyang’anira zinthu za mfumu. 60 Yeremiya analemba m’buku limodzi+ za masoka onse odzagwera Babulo. Iye analemba mawu onsewa okhudza zimene zidzachitikire Babulo. 61 Chotero Yeremiya anauza Seraya kuti: “Ukakafika ku Babulo ndi kuona mzindawo, ukawerenge mokweza mawu onsewa.+ 62 Ukanene kuti, ‘Inu Yehova! Inu mwanena zowononga malo ano ndi kuwafafaniza kuti pasapezekenso chilichonse chokhalamo.+ Musapezeke munthu kapena chiweto koma mzindawo ukhale bwinja mpaka kalekale.’ 63 Ndiye ukakamaliza kuwerenga bukuli, ukalimangirire mwala ndi kuliponya pakati pa mtsinje wa Firate.+ 64 Ndiyeno ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene Babulo adzamirire osatulukanso chifukwa cha masoka amene ndikumugwetsera.+ Ndipo Ababulowo adzadzitopetsa okha.’”+

Mawu a Yeremiya athera pamenepa.

52 Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira,+ ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Libina,+ ndipo dzina lawo linali Hamutali,+ mwana wa Yeremiya. 2 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu+ anachita. 3 Zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda zinakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.+ 4 Ndiyeno m’chaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya,+ m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwera ku Yerusalemu+ kudzaukira mzindawo. Atafika anayamba kumanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+ 5 Choncho mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.+

6 M’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo, ndipo anthu a m’dzikolo analibiretu chakudya.+ 7 Ndiyeno khoma la mzindawo linabooledwa,+ ndipo amuna onse ankhondo anayamba kuthawa.+ Iwo anatuluka mumzindawo usiku kudzera pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu,+ ndipo analowera njira yopita ku Araba. Apa n’kuti Akasidi atazungulira mzinda wonsewo.+ 8 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linayamba kuthamangitsa mfumuyo+ ndipo Zedekiya anamupeza+ m’chipululu cha Yeriko. Zitatero gulu lonse lankhondo la Zedekiya linabalalika n’kumusiya yekha.+ 9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo n’kupita nayo ku Ribila,+ kwa mfumu ya Babulo,+ m’dziko la Hamati,+ kuti mfumu ya Babuloyo ikamuweruze.+ 10 Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, iye akuona.+ Inaphanso akalonga onse a ku Yuda.+ 11 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga ndi maunyolo amkuwa n’kupita naye ku Babulo.+ Kumeneko anamuika m’ndende mpaka tsiku la imfa yake.

12 Ndiyeno m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Mfumu Nebukadirezara+ ya Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali kutumikira mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu. 13 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ Anatenthanso nyumba iliyonse ya munthu wotchuka.+ 14 Kenako gulu lonse lankhondo la Akasidi, lomwe linali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, linagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+

15 Anthu onyozeka pakati pa Ayudawo, anthu ena onse amene anatsala mumzindamo,+ anthu amene anathawira ku mbali ya mfumu ya Babulo ndi amisiri onse aluso, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+ 16 Ena mwa anthu onyozeka a m’dzikolo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi alimi ogwira ntchito mokakamizidwa.+

17 Zipilala zamkuwa+ zimene zinali panyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wakewo kupita nawo ku Babulo.+ 18 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo,+ zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ makapu ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ansembe anali kugwiritsira ntchito potumikira.+ 19 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga mabeseni,+ zopalira moto, mbale zolowa,+ ndowa zochotsera phulusa, zoikapo nyale,+ zikho ndi mbale zinanso zolowa zomwe zinali zagolide weniweni,+ komanso zomwe zinali zasiliva weniweni.+ 20 Koma panalibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa zipilala ziwiri zija,+ chosungiramo madzi chimodzi chija,+ ng’ombe zamkuwa 12+ zija ndi zotengera zokhala ndi mawilo zimene Mfumu Solomo inapangira nyumba ya Yehova.+ Palibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa ziwiya zonsezi.+

21 Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chotalika mikono* 18,+ ndipo chinali kuzunguliridwa ndi chingwe chotalika mikono 12.+ Chipilala chilichonse chinali champhako ndipo kuchindikala kwake kunali kofanana ndi mphipi ya zala zinayi. 22 Mutu wa chipilala chilichonse unali wamkuwa.+ Mutuwo kutalika kwake kunali mikono isanu,+ ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo,+ onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa komanso chinali ndi makangaza.+ 23 Makangaza amene anali m’mbali mwa zipilalazo analipo 96, ndipo makangaza onse amene anali pamaukondewo analipo 100.+

24 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri, ndi alonda atatu a pakhomo.+ 25 Mumzindawo anatengamo nduna imodzi ya panyumba ya mfumu imene inali kuyang’anira amuna ankhondo. Anatenganso amuna 7 kuchokera pa anthu amene ankatha kuonana ndi mfumu mwa amuna amene anali mumzindamo.+ Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe anali kusonkhanitsa ankhondo a m’dzikolo, ndi amuna 60 mwa anthu a m’dzikolo amene anali mumzindawo.+ 26 Choncho, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa n’kupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 27 Mfumu ya Babulo inapha anthu amenewa+ ku Ribila+ m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+

28 Ziwerengero za anthu amene Nebukadirezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi izi: m’chaka cha 7 cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023.+

29 M’chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadirezara,+ anatenga anthu 832 kuchokera ku Yerusalemu.

30 M’chaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadirezara, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga Ayuda 745 kupita nawo ku ukapolo.+

Anthu onse amene anawatenga anali 4,600.

31 Kenako, m’chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 12, pa tsiku la 25 la mweziwo, chaka chimene Evili-merodaki mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende.+ 32 Kenako anayamba kulankhula naye zinthu zabwino, ndipo anakweza ufumu wake kuposa mafumu ena amene anali naye limodzi ku Babulo.+ 33 Yehoyakini anavula zovala zake za kundende,+ ndipo nthawi zonse anali kudya chakudya+ pamaso pa mfumuyo masiku onse a moyo wake.+ 34 Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumu ya Babulo, masiku onse a moyo wake. Anali kumupatsa chakudya chimenechi tsiku ndi tsiku mpaka imfa yake.+

Dzinali limatanthauza “Ya Amamasula [mimba]”; kapena, “Ya Amakweza.”

Dzinali limatanthauza “Gawo Langa Ndi Yehova.”

Umenewu ndi mwezi wa Abi. Onani Zakumapeto 13.

M’Chiheberi mawu akuti “mtengo wa amondi” amatanthauza “wogalamuka” chifukwa chakuti ndi umodzi mwa mitengo yoyambirira kutulutsa maluwa. Izi zikugwirizana ndi mawu a Yehova pa vesi 12.

Onani mawu a m’munsi pa vesi 11.

Mawu ake enieni, “anakudya paliwombo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “uli ndi nkhope ya mkazi wochita uhule.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “idzadzidalitsa yokha.”

Ena amati “masaka.”

Ena amati “kugwaza.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”

Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Ena amati “nyalugwe.”

Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Munthu “wachisasati” ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Tikati nthungo tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.

Ena amati “saka.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”

Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.

Kapena kuti “Mwitiyopiya.”

Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.

Mawu ake enieni, “chinyengo.”

Kapena kuti, “ndi wosowa pogwira,” ndi “woopsa.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Kapena kuti “ku Negebu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “musaphimbe.”

Chipatachi chiyenera kuti ndi chimene chinali kutchedwa kuti “Chipata cha Milu ya Phulusa.”

Mawu ake enieni, “ndauikira nkhope yanga motsutsana nawo.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Mawu ake enieni, “kulemera.” Mawu achiheberi otanthauza “katundu wolemetsa” ali ndi matanthauzo awiri. Panopa m’lembali akutanthauza uthenga wamphamvu wochokera kwa Mulungu, koma pamalo otsatira m’lemba lomweli akutanthauza kuti anthuwo anali katundu wolemetsa kwa Mulungu. Choncho poyankha, Yeremiya anagwiritsa ntchito mawuwa chifukwa cha matanthauzo ake awiriwa.

Mawu ake enieni, “nyanja.”

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.

Mano amayayamira munthu akadya zinthu zowawasa. Ena amati “kuchita dziru.”

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Mawu ake enieni, “pachifuwa cha ana awo.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Umenewu ndi mwezi wa Kisilevu, dzina la mwezi wa 9 pakalendala yachiyuda imene anali kuigwiritsa ntchito atabwera kuchokera ku ukapolo. Mweziwu unali kuyamba chakumapeto kwa November mpaka pakati pa December. Onani Zakumapeto 13.

Pa dzina lakuti “Mwitiyopiya” m’Chiheberi pali mawu akuti “Mkusi.”

Kapena kuti “mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu.”

Kapena kuti “mkulu wa azamatsenga (wolosera zam’tsogolo, wopenda nyenyezi), mkulu wa akuluakulu.”

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.

Mawu ake enieni, “Nyumba ya Dzuwa.”

Mawu ake enieni, “ndakuikirani nkhope yanga motsutsana nanu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti “odula nkhuni.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.

Mawu ake enieni, “ana anu aamuna opanda abambo.”

Mawu ake enieni, “kumphepo zonse,” kutanthauza kumbali zonse kumene mphepo imapita.

Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena